Yobu
24 “N’chifukwa chiyani Wamphamvuyonse sanakhazikitse nthawi yachiweruzo,+
Ndipo n’chifukwa chiyani omudziwa sanaone masiku ake achiweruzo?+
3 Amathamangitsa ngakhale bulu wamphongo wa ana amasiye,*
Amalanda ng’ombe yamphongo ya mkazi wamasiye ngati chikole.+
Osaukawo amapita kukafunafuna chakudya.
Chipululu chimapatsa aliyense chakudya cha ana ake.
6 M’munda wa munthu wina, osauka amakololamo chakudya cha ziweto,
Ndipo iwo amalanda msangamsanga zinthu za m’munda wa mpesa wa munthu woipa.
8 Amanyowa ndi mvula yamkuntho ya m’mapiri,
Ndipo chifukwa chakuti alibe pobisala,+ amakupatira thanthwe.
9 Oipa amalanda mwana wamasiye kum’chotsa pabere.+
Amatenga ngati chikole chovala chimene wozunzika wavala.+
12 Anthu amene akufa amamveka kubuula kunja kwa mzinda,
Moyo wa anthu amene akufa chifukwa chovulala umafuula popempha thandizo,+
Ndipo Mulungu saziona ngati zolakwika.+
13 Oipawo amasonyeza kuti ali pakati pa opanduka omwe amatsutsana ndi kuwala.+
Iwo sanazindikire njira zake,
Ndipo sanakhale m’misewu yake.
14 Kukangocha, wakupha amadzuka
Kupita kukapha wozunzika ndi wosauka,+
Ndipo usiku iye amakhala wakuba.+
15 Diso la wachigololo+ limadikira kuti mdima ugwe madzulo.+
Iye amati, ‘Palibe diso limene lindione,’+
Ndipo amaphimba kumaso kwake.
16 Mu mdima iye amathyola nyumba za anthu,
Masana iwo amadzitsekera m’nyumba,
Ndipo saona kuwala kwa masana.+
17 Kwa iwo m’mawa n’chimodzimodzi ndi mdima wandiweyani,+
Chifukwa zoopsa zadzidzidzi za mu mdima wandiweyani amazidziwa.
18 Woipa amatengedwa mwamsanga ndi madzi.
Malo awo adzakhala otembereredwa padziko lapansi.+
Sadzapatukira kunjira yopita kuminda ya mpesa.
19 Chilala ndi kutentha zimatenga madzi a chipale chofewa.
Ndi mmenenso Manda amachitira ndi anthu amene achimwa.+
20 Mimba idzamuiwala, mphutsi zidzamumva kutsekemera pomuyamwa,+
Ndipo iye sadzakumbukiridwanso.+
Kupanda chilungamo kudzathyoledwa ngati mtengo.+
21 Woipa amachita zoipa ndi mkazi wouma amene sabereka,
Komanso ndi mkazi wamasiye+ amene woipayo sam’chitira zabwino.
22 Ndi mphamvu zake, Mulungu adzakoka anthu anyonga.
Oipa adzakhala apamwamba n’kumakayikira za moyo wawo.
23 Mulungu adzachititsa oipawo kuti azidzidalira+ n’cholinga choti azitha kudzisamalira.
Maso ake adzakhala panjira zawo.+
24 Oipawo amakhala okwezeka kwa kanthawi, kenako n’kutha.+
Iwo amatsitsidwa,+ ndipo mofanana ndi wina aliyense amathotholedwa.
Amadulidwa mofanana ndi nsonga ya ngala za tirigu.
25 Choncho ndani amene anganene kuti ndine wabodza?
Kapena kunena kuti mawu anga ndi achabechabe?”