Yobu
12 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Zoonadi, amuna inu ndinu anthu,
Ndipo nzeru zidzathera limodzi ndi inu.+
3 Inenso ndili ndi zolinga zabwino+ ngati inuyo.
Si ine wonyozeka kwa inu,+
Ndipo ndani amene alibe zinthu ngati zimenezi?
4 Ine ndakhala chinthu choseketsa kwa anthu anzanga,+
Ndakhala munthu woitana kwa Mulungu kuti amuyankhe.+
Munthu wolungama ndi wosalakwa wakhala choseketsa.
5 Amene ali pa mtendere amanyoza tsoka n’kumaganiza kuti+
Limagwera okhawo amene mapazi awo amaterereka.+
6 Mahema a anthu olanda amakhala opanda nkhawa,+
Ndipo anthu okwiyitsa Mulungu amakhala pa mtendere
Wofanana ndi wa munthu amene watenga mulungu* m’manja mwake.+
9 Ndani pa zonsezi sadziwa bwino
Kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi?+
10 Iye amene moyo+ wa aliyense uli m’dzanja lake,
Ndiponso mzimu wa anthu onse.+
11 Kodi khutu si paja limasiyanitsa mawu+
Ngati mmene m’kamwa+ mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya?
12 Kodi okalamba si paja amakhala ndi nzeru,+
Ndipo amene akhala masiku ambiri si paja amamvetsa zinthu?
14 Iyetu amagwetsa zinthu kuti zisamangidwe,+
Zimene iye watseka, palibe munthu amene angazitsegule.+
16 Iye ali ndi mphamvu ndi nzeru zopindulitsa.+
Kwa iye kuli wochimwa mosazindikira ndi wochimwitsa ena.+
17 Amachititsa alangizi kuyenda opanda nsapato,+
Ndipo oweruza amawachititsa misala.
19 Amachititsa ansembe kuyenda opanda nsapato,+
Ndipo amene akhazikika amawawononga.+
20 Okhulupirika, iye amawakhalitsa chete,
Ndipo amuna okalamba, iye amawachotsera nzeru.
21 Iye amanyoza anthu olemekezeka,+
Ndipo amakhwepetsa lamba wa anthu amphamvu.
22 Amavundukula zinthu zozama zimene zinali pamdima,+
Ndipo amaunika pamdima wandiweyani.
23 Amapatsa mphamvu mitundu kuti aiwononge.+
Amafutukula mitundu kuti aichotse.
24 Amachotsa nzeru za atsogoleri a anthuwo,
Kuti iwo aziyendayenda kumalo kopanda kanthu,+ kumene kulibe njira.