1 Mbiri
17 Ndiyeno Davide atangoyamba kukhala m’nyumba yake,+ anauza Natani+ mneneri kuti: “Ine ndikukhala m’nyumba ya mitengo ya mkungudza,+ koma likasa+ la pangano la Yehova likukhala m’chihema chansalu.”+ 2 Pamenepo Natani anauza Davide kuti: “Chitani chilichonse chimene chili mumtima mwanu,+ chifukwa Mulungu woona ali nanu.”+
3 Tsopano usiku umenewo, Mulungu analankhula+ ndi Natani, kuti: 4 “Pita, ukauze Davide mtumiki wanga kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Si iwe amene udzandimangira nyumba yokhalamo.+ 5 Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa Isiraeli mu Iguputo kufikira lero,+ sindinakhalepo m’nyumba, koma ndakhala m’hema ndi m’hema ndiponso m’chihema chopatulika+ ndi m’chihema chopatulika.+ 6 Pa nthawi yonse imene ndinali kuyendayenda+ pakati pa Isiraeli yense, kodi ndinalankhulapo n’kamodzi komwe kwa woweruza aliyense wa Isiraeli, amene ndinalamula kutsogolera anthu anga, mawu akuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu inu simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”’+
7 “Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unali kusamalira nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri+ wa anthu anga Aisiraeli. 8 Ine ndidzakhala ndi iwe kulikonse kumene udzapite,+ ndipo ndidzawononga ndi kuchotsa adani ako onse+ pamaso pako. Ndidzakupangira dzina+ lofanana ndi dzina la anthu otchuka amene ali padziko lapansi.+ 9 Ndipo anthu anga Aisiraeli ndidzawasankhira malo ndi kuwakhazika pamalowo.+ Iwo adzakhaladi kumeneko ndipo sadzasokonezedwanso. Anthu osalungama+ sadzawavutitsanso ngati mmene anachitira poyamba,+ 10 ngati mmene anachitira kuchokera masiku amene ndinaika oweruza+ kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli. Ndipo ndidzatsitsa adani ako onse.+ Tsopano ndikukuuza kuti: ‘Kuwonjezera pamenepo, Yehova adzakumangira nyumba.’*+
11 “‘“Masiku ako akadzakwana kuti ukakhale pamodzi ndi makolo ako,+ pamenepo ndithu ndidzautsa mbewu yako yobwera pambuyo pako,+ imene idzakhala mmodzi wa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.+ 12 Iye ndiye adzandimangire nyumba,+ ndipo ndithu ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+ 13 Ine ndidzakhala atate wake+ ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Sindidzachotsa kukoma mtima kwanga kosatha pa iye+ monga mmene ndinachitira kwa amene analipo iwe usanakhalepo.+ 14 Ndidzamukhazikitsa iye kukhala woyang’anira nyumba yanga+ ndi ufumu wanga+ mpaka kalekale, ndipo mpando wake wachifumu+ sudzatha mpaka kalekale.”’”
15 Natani anauza Davide mawu onsewa ndi masomphenya onse amene anaona.+
16 Pamenepo Mfumu Davide inabwera ndi kukhala pansi pamaso pa Yehova,+ ndipo inati: “Ndine yani ine,+ inu Yehova Mulungu? Ndipo nyumba yanga n’chiyani+ kuti mundifikitse pamene ndili pano?+ 17 Inu Mulungu,+ kuwonjezeranso pamenepa+ mwandiuza kuti nyumba ya ine mtumiki wanu idzakhazikika mpaka nthawi yam’tsogolo,+ ndipo inu Yehova Mulungu, mwanditenga ine ngati munthu woyenera kukwezedwa.+ 18 Ndiyeno ine Davide ndinganenenji kwa inu poona kuti mwandilemekeza ine mtumiki wanu,+ pamene inu mumandidziwa bwino ine mtumiki wanu?+ 19 Inu Yehova, chifukwa cha ine mtumiki wanu, komanso mogwirizana ndi zofuna za mtima wanu,+ mwachita zazikulu zonsezi mwa kundidziwitsa zinthu zonse zazikulu zimene mudzachita.+ 20 Inu Yehova, palibe wofanana nanu,+ ndipo malinga ndi zonse zimene tamva ndi makutu athu, palibenso Mulungu wina koma inu nokha.+ 21 Ndi mtundu winanso uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu woona munawawombola monga anthu anu,+ ndi kudzipangira dzina mwa kuchita zinthu zazikulu+ ndi zochititsa mantha, popitikitsa mitundu+ pamaso pa anthu anu amene munawawombola ku Iguputo? 22 Inutu munapanga anthu anu Aisiraeli kuti akhaledi anthu anu+ mpaka kalekale. Ndipo inu Yehova munakhala Mulungu wawo.+ 23 Tsopano inu Yehova, mawu amene mwalankhula okhudza mtumiki wanu ndi nyumba yake, akhale oona mpaka kalekale, ndipo chitani mmene mwanenera. 24 Dzina lanu+ likhale lokhulupirika ndi lokwezeka+ mpaka kalekale. Anthu anene kuti, ‘Yehova wa makamu+ Mulungu wa Isiraeli,+ ndiye Mulungu wa Isiraeli,’+ ndipo nyumba ya mtumiki wanu Davide ikhalitse pamaso panu.+ 25 Pakuti inu Mulungu wanga mwandiululira ine mtumiki wanu cholinga chanu chondimangira nyumba,+ n’chifukwa chake ine mtumiki wanu ndapeza nthawi yopemphera pamaso panu. 26 Tsopano inu Yehova, ndinu Mulungu woona,+ ndipo mwandilonjeza ine mtumiki wanu zabwino zimenezi.+ 27 Choncho dalitsani nyumba ya mtumiki wanu kuti ikhazikike pamaso panu mpaka kalekale.+ Pakuti inu Yehova mwadalitsa nyumba ya mtumiki wanu, ndipo yadalitsika mpaka kalekale.”+