2 Mafumu
3 Yehoramu+ mwana wa Ahabu, anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya m’chaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya Yuda, ndipo analamulira kwa zaka 12. 2 Iye anali kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ koma osati ngati mmene anachitira bambo ake+ kapenanso mmene anachitira mayi ake. Iye anachotsa chipilala chopatulika+ cha Baala chimene bambo ake anapanga.+ 3 Komabe, anaumirira osasiya kuchita machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa+ nawo Isiraeli.
4 Mesa+ mfumu ya Mowabu anali woweta nkhosa. Ankapereka kwa mfumu ya Isiraeli ana a nkhosa 100,000, ndi nkhosa zamphongo zosameta ubweya zokwana 100,000 monga msonkho. 5 Ahabu atangomwalira,+ mfumu ya Mowabu inapandukira+ mfumu ya Isiraeli. 6 Pa nthawiyo, Mfumu Yehoramu inatuluka ku Samariya n’kukasonkhanitsa+ Aisiraeli onse. 7 Kuwonjezera apo, inatumiza uthenga kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, wakuti: “Mfumu ya Mowabu yandipandukira. Kodi upita nane kukamenya nkhondo ku Mowabu?” Yehosafati anayankha kuti: “Inde ndipita.+ Iwe ndi ine ndife amodzi. Anthu ako ndi anthu anga ndi amodzi.+ Mahatchi anga n’chimodzimodzi ndi mahatchi ako.” 8 Yehosafati anafunsa kuti: “Tidzera njira iti?” Yehoramu anayankha kuti: “Tidzera njira ya m’chipululu cha Edomu.”+
9 Choncho mfumu ya Isiraeli, mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu+ ananyamuka n’kuyenda mozungulira kwa masiku 7. Koma kuchipululuko kunalibe madzi oti anthuwo amwe pamodzi ndi ziweto zimene anali kuyenda nazo. 10 Kenako mfumu ya Isiraeli inati: “Kalanga ine! Yehova wasonkhanitsa ife mafumu atatu kuti atipereke m’manja mwa Mowabu!”+ 11 Pamenepo Yehosafati anati:+ “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova?+ Ngati alipo tiyeni tifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye.”+ Ndiyeno mmodzi mwa atumiki a mfumu ya Isiraeli anayankha kuti: “Kuli Elisa+ mwana wa Safati, amene anali kuthirira Eliya madzi osamba m’manja.”+ 12 Atamva zimenezo, Yehosafati anati: “Mawu a Yehova ali mwa iye.” Choncho mfumu ya Isiraeli, Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anapita kwa Elisa.
13 Elisa anafunsa mfumu ya Isiraeli kuti: “Ndili nanu chiyani?+ Pitani kwa aneneri+ a bambo anu ndi kwa aneneri a mayi anu.” Koma mfumu ya Isiraeliyo inati: “Ayi musatero, chifukwa Yehova wasonkhanitsa ife mafumu atatu kuti atipereke m’manja mwa Mowabu.”+ 14 Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova wa makamu Mulungu wamoyo amene ndimam’tumikira,+ pakanakhala kuti palibe Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikanakuyang’anani+ n’komwe kapena kukusamalani.+ 15 Anthu inu, ndiitanireni woimba zeze.”+ Woimba zezeyo atangoyamba kuimba, dzanja+ la Yehova linakhala pa Elisa. 16 Kenako iye anati: “Yehova wanena kuti, ‘Mukumbekumbe ngalande m’chigwa* chonsechi,+ 17 chifukwa Yehova wanena kuti: “Anthu inu simuona mphepo kapena mvula, koma chigwa chonsechi chidzaza madzi.+ Inu pamodzi ndi ziweto zanu, ndithu mumwa madziwo.”’+ 18 Zimenezi ndi zinthu zazing’ono kwambiri pamaso pa Yehova,+ ndipo ndithu apereka Amowabu m’manja mwanu.+ 19 Choncho mukagwetse mzinda uliwonse wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri,+ mzinda uliwonse wabwino kwambiri,+ ndi mtengo uliwonse wabwino.+ Mukatseke akasupe onse amadzi, ndipo mukawononge malo alionse abwino mwa kuponyapo miyala.”
20 Ndiyeno zinachitika n’zakuti, pa nthawi yopereka nsembe yambewu+ m’mawa,+ anangoona madzi akuyenda kuchokera cha ku Edomu, ndipo malo onsewo anadzaza madzi.
21 Amowabu onse atamva kuti kwabwera mafumu kudzamenyana nawo, anasonkhanitsa amuna ambiri kuyambira amsinkhu wopita ku nkhondo+ kupita m’tsogolo, ndipo anakaima m’malire. 22 Atadzuka m’mawa, dzuwa linawalira pamadzi aja, moti kwa Amowabu amene anali kutsidya linalo, madziwo anaoneka ofiira ngati magazi. 23 Ataona zimenezi, anayamba kunena kuti: “Amenewa ndi magazi. Ndithu mafumu aja aphedwa ndi lupanga. Ndiye kuti aphana okhaokha. Tsopano Amowabu inu, tiyeni tikafunkhe!”+ 24 Iwo atalowa mumsasa wa Aisiraeli,+ nthawi yomweyo Aisiraeli ananyamuka n’kuyamba kuwapha. Amowabuwo anayamba kuthawa,+ ndipo Aisiraeli anathamangitsa Amowabuwo n’kumawapha mpaka kukalowa ku Mowabu. 25 Ndiyeno Aisiraeliwo anayamba kugwetsa mizinda.+ Pamalo alionse abwino, aliyense anali kuponyapo mwala mpaka kudzaza malo onsewo. Anatseka kasupe aliyense wamadzi+ ndi kugwetsa mtengo uliwonse wabwino.+ Koma miyala ya mzinda wa Kiri-hareseti+ yokha anaisiya. Oponya miyala anazungulira mzindawo n’kuuponya miyala.
26 Mfumu ya Mowabu itaona kuti nkhondo yaikulira, nthawi yomweyo inatenga amuna 700 amalupanga pofuna kudutsa kuti ikapeze mfumu ya Edomu,+ koma iwo analephera. 27 Pomalizira pake, mfumu ya Mowabu inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa amene akanalowa ufumu m’malo mwake, n’kumupereka+ nsembe yopsereza pakhoma. Choncho panabuka mkwiyo waukulu kwambiri wokwiyira Aisiraeli, motero iwo analeka kumenyana ndi mfumu ya Mowabu ndipo anabwerera kwawo.