Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Malachi 1:1-4:6
  • Malaki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malaki
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Malaki

Malaki

1 Uthenga wokhudza Isiraeli:

Nawa mawu a Yehova+ onena za Isiraeli kudzera mwa Malaki:

2 Yehova wanena kuti: “Ine ndimakukondani anthu inu.”+

Koma inu mwanena kuti: “Mumatikonda motani?”+

“Kodi Esau sanali m’bale wake wa Yakobo?+ Koma ine ndinakonda Yakobo,”+ watero Yehova. 3 “Esau+ ndinadana naye. Pamapeto pake, mapiri ake ndinawasandutsa bwinja.+ Malo ake okhala, ine ndinawasandutsa malo okhala mimbulu ya m’chipululu.”+

4 “Popeza kuti Edomu akunena kuti, ‘Ife tawonongedwa, koma tibwerera ndi kukamanga malo athu owonongedwawo,’ Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Iwo akamanga, koma ine ndikagwetsa.+ Anthu adzatcha malo awowo, “dera la zoipa” ndipo iwowo adzatchedwa, “anthu okanidwa ndi Yehova+ mpaka kalekale.”* 5 Inu mudzaona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati: “Yehova atamandike m’dera lonse la Isiraeli.”’”+

6 “‘Mwana amalemekeza bambo ake+ ndipo wantchito amalemekeza mbuye wake.+ Ngati ine ndili atate,+ ulemu wanga uli kuti?+ Ngati ndili Ambuye Wamkulu, n’chifukwa chiyani simundiopa?’+ watero Yehova wa makamu kwa inu ansembe amene mukunyoza dzina langa.+

“‘Inu mukunena kuti: “Kodi dzina lanu talinyoza motani?”’

7 “‘Mwalinyoza mwa kupereka nsembe zodetsedwa paguwa langa lansembe.’+

“‘Inu mukunena kuti: “Takudetsani motani?”’

“‘Mwandidetsa ponena kuti: “Tebulo+ la Yehova ndi lonyozeka.”+ 8 Mukapereka nsembe nyama yakhungu, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.” Mukapereka nsembe nyama yolumala kapena yodwala, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.”’”+

“Pitani nayo kwa bwanamkubwa wanu. Kodi akakondwera nanu? Kapena kodi akakulandirani bwino?” watero Yehova wa makamu.

9 “Tsopano khazikani pansi mtima+ wa Mulungu kuti atichitire chifundo.+ Mukuchita zoipazi ndi manja anu. Kodi Mulungu angalandire aliyense wa inu?” watero Yehova wa makamu.

10 “Ndani pakati panu amene angatseke zitseko za kachisi popanda malipiro?+ Anthu inu mumayatsa moto paguwa langa lansembe kuti mulandire malipiro.+ Ine sindikukondwera nanu, ndipo nsembe zanu zimene mukupereka monga mphatso sizikundisangalatsa,”+ watero Yehova wa makamu.

11 “Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera, dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.+ Kulikonse anthu azidzapereka nsembe zautsi.+ Anthu azidzapereka zopereka kapena kuti mphatso zovomerezeka polemekeza dzina langa.+ Adzachita izi chifukwa dzina langa lidzakhala lokwezeka pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu.

12 “Koma anthu inu mukundinyoza+ mwa kunena kuti, ‘Palibe vuto kudetsa tebulo la Yehova, ndipo zopereka kapena kuti chakudya chimene chili pamenepo n’chonyozeka.’+ 13 Inu mumanena kuti, ‘Koma ndiye n’zotopetsa bwanji!’+ Ndipo mumanunkhiza nsembezo monyansidwa,” watero Yehova wa makamu. “Inu mumabweretsa nyama zobedwa, zolumala ndi zodwala.+ Mumapereka zimenezi ngati mphatso. Kodi zopereka zanu zoterezi ine ndingakondwere nazo?”+ watero Yehova.

14 “Aliyense wochita zachinyengo popereka nsembe nyama yachilema ndi wotembereredwa. Iye amalonjeza ndi kupereka nsembe nyama yachilema kwa Yehova pamene nyama yamphongo yabwinobwino, ali nayo pagulu la ziweto zake.+ Ine ndine Mfumu yaikulu+ ndipo dzina langa lidzaopedwa pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu.

2 “Tsopano lamulo ili ndi la inu ansembe.+ 2 Mukapanda kumvera,+ ndiponso ngati simuganizira nkhani imeneyi mumtima mwanu+ kuti mulemekeze dzina langa,+ ndidzakutumizirani temberero+ ndi kutemberera madalitso anu.+ Ndatemberera dalitso la aliyense wa inu chifukwa simunaganizire nkhani imeneyi mumtima mwanu,” watero Yehova wa makamu.

3 “Tamverani! Ndiwononga mbewu chifukwa cha inu+ ndipo ndikuwazani ndowe kumaso. Ndikuwazani ndowe za nyama zimene mumapereka nsembe pa zikondwerero zanu. Munthu wina adzakunyamulani ndi kukakutayani pandowezo. 4 Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndakutumizirani lamulo limeneli+ kuti pangano+ limene ndinapangana ndi Levi lipitirire,”+ watero Yehova wa makamu.

5 “Pangano limene ndinapangana naye linasunga moyo wake. Linamuthandizanso kukhala ndi moyo wamtendere.+ Chifukwa cha madalitso amenewa, anali kundiopa.+ Popeza kuti anali kulemekeza dzina langa, sankachita chilichonse chondikwiyitsa.+ 6 Lamulo la choonadi linali m’kamwa mwake+ ndipo pamilomo pake panalibe zosalungama. Anali kuyenda ndi ine mwamtendere komanso mowongoka mtima,+ ndipo anabweza anthu ambiri panjira zawo zolakwika.+ 7 Wansembe ayenera kuphunzitsa anthu kuti adziwe Mulungu. Anthuwo ayenera kufunafuna kumva chilamulo kuchokera pakamwa pake,+ pakuti iye ndi mthenga wa Yehova wa makamu.+

8 “Koma inu mwapatuka panjira yoyenera.+ Mwalepheretsa anthu ambiri kutsatira chilamulo.+ Mwaphwanya pangano limene ndinapangana ndi Levi,”+ watero Yehova wa makamu. 9 “Inenso ndidzachititsa kuti inu mukhale anthu onyozeka ndi otsika kwa anthu onse,+ chifukwa simunayende m’njira zanga, koma munali kukondera pa nkhani zokhudza chilamulo.”+

10 “Kodi tonsefe atate wathu si mmodzi?+ Kodi si Mulungu mmodzi amene anatilenga?+ N’chifukwa chiyani tikuchitirana zachinyengo,+ mwa kuipitsa pangano la makolo athu akale?+ 11 Yuda wachita zachinyengo, ndipo mu Isiraeli ndi mu Yerusalemu mwachitika zinthu zonyansa.+ Pakuti Yuda wadetsa chiyero cha Yehova+ chimene Mulungu amachikonda, ndipo Yuda wakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.+ 12 Yehova adzapha ndi kuchotsa munthu aliyense wochita zonyansazi+ m’mahema a Yakobo. Iye adzapha ndi kuchotsamo aliyense, kaya akhale ndani.* Komanso adzapha aliyense amene akupereka nsembe ngati mphatso+ kwa Yehova wa makamu.”

13 “Pali chinthu china chimene anthu inu mukuchita ndipo chikuchititsa kuti guwa lansembe la Yehova lidzaze ndi misozi, kulira ndi kubuula. Chifukwa cha zimenezi, nsembe zanu zimene mumapereka ngati mphatso n’zosavomerezeka kwa iye ndipo sakusangalala ndi chilichonse chochokera m’manja mwanu.+ 14 Inu mwanena kuti, ‘Chifukwa chiyani?’+ Chifukwa chakuti Yehova wakudzudzulani popeza kuti aliyense wa inu wachitira zachinyengo mkazi amene anamukwatira ali mnyamata,+ ngakhale kuti iye anali mnzake komanso mkazi wa pangano lake.+ 15 Komabe pakati panu pali ena amene atsimikiza mtima kuti asachite zoterezi. Iwo akufuna kukhala ndi ana amene angakhaledi anthu a Mulungu.*+ Mphamvu ya Mulungu ikutsogolera anthu amenewa pa zonse zimene akuchita. Tsopano inunso ganizirani mofatsa ndipo mukhale ndi maganizo oyenera.+ Tsimikizani mtima kuti musachitire zachinyengo akazi anu amene munawakwatira muli anyamata.+ 16 Pakuti ine ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja,”+ watero Yehova Mulungu wa Isiraeli. “Ndimadana ndi munthu amene zochita zake zankhanza zili ngati chovala chauve chimene wavala.+ Musamale ndi maganizo a mumtima mwanu ndipo musamachite zachinyengo,”+ watero Yehova wa makamu.

17 “Anthu inu mwatopetsa Yehova ndi mawu anu,+ ndipo mwanena kuti, ‘Tamutopetsa motani?’ Mwa kunena kuti, ‘Aliyense wochita zoipa ndi wabwino kwa Yehova, ndipo iye amakondwera ndi anthu otero.’+ Kapena mwa kunena kuti, ‘Kodi Mulungu wachilungamo ali kuti?’”+

3 “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga+ ndipo iye adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi+ Wake.+ Adzabwera ndi mthenga+ wa pangano+ amene mukumuyembekezera mosangalala.+ Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa makamu.+

2 “Ndani adzapirire pa tsiku limene adzabwere?+ Ndipo ndani adzaime chilili iye akadzaonekera?+ Iye adzakhala ngati moto wa woyenga zitsulo+ komanso ngati sopo+ wa ochapa zovala.+ 3 Iye adzakhala pansi ngati woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeretsa siliva.+ Adzayeretsa ana a Levi+ ndipo adzawayeretsa ngati golide+ ndi siliva. Pamene azidzapereka nsembe zawo ngati mphatso, Yehova adzaona kuti nsembe zawozo akuzipereka+ molungama. 4 Nsembe zimene Yuda ndi Yerusalemu adzapereke monga mphatso, zidzasangalatsa Yehova,+ ngati mmene zinalili kalekale kapena kuti nthawi zamakedzana.+

5 “Anthu inu ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni.+ Sindidzazengereza kupereka umboni+ wotsutsa amatsenga,+ achigololo,+ olumbira monama+ komanso ochita chinyengo pa malipiro a munthu waganyu.+ Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa anthu ochitira chinyengo mkazi wamasiye,+ mwana wamasiye*+ ndiponso opondereza alendo.+ Anthu amenewa sakundiopa,”+ watero Yehova wa makamu.

6 “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.+ Inu ndinu ana a Yakobo ndipo simunatheretu.+ 7 Kuyambira m’masiku a makolo anu mwakhala mukupatuka pa malamulo anga ndipo simunawasunge.+ Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu,”+ watero Yehova wa makamu.

Koma inu mukunena kuti: “Tibwerere motani?”

8 “Kodi munthu wochokera kufumbi angabere Mulungu? Komatu inu mukundibera.”

Inu mukunena kuti: “Takuberani motani?”

“Mukundibera kudzera m’chakhumi* ndi m’zopereka. 9 Inu mukundinyoza kwambiri+ ndipo mukundibera. Mtundu wanu wonsewu ukuchita zimenezi. 10 Bweretsani gawo limodzi mwa magawo 10 alionse a zinthu zanu+ n’kuziika mosungiramo zinthu zanga, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya.+ Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi,+ kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba+ ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira,”+ watero Yehova wa makamu.

11 “Ine ndidzakudzudzulirani dzombe,+ ndipo silidzawononganso mbewu za m’munda mwanu. Mitengo ya mpesa ya m’munda mwanu izidzabereka zipatso nthawi zonse,”+ watero Yehova wa makamu.

12 “Mitundu ina yonse ya anthu idzakutchani odala,+ pakuti mudzakhala dziko losangalatsa,”+ watero Yehova wa makamu.

13 “Inu mwandinenera mawu achipongwe,”+ watero Yehova.

Koma mukunena kuti: “Ife takunenerani zachipongwe zotani?”+

14 “Inu mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu n’kopanda phindu.+ Tapindulanji chifukwa chomutumikira ndiponso chifukwa choyenda mwachisoni pamaso pa Yehova wa makamu?+ 15 Panopa anthu odzikuza tikuwatcha odala.+ Komanso anthu ochita zoipa zinthu zikuwayendera bwino.+ Iwo ayesa Mulungu koma sakulandira chilango.’”+

16 Pa nthawi imeneyo anthu oopa Yehova+ analankhulana, aliyense ndi mnzake, ndipo Yehova anatchera khutu ndi kumvetsera.+ Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake.+ Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizira za dzina lake.+

17 “Iwo adzakhala anthu anga,+ pa tsiku limene ndidzawasandutse chuma chapadera,”+ watero Yehova wa makamu. “Ndidzawachitira chifundo monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.+ 18 Ndithu, anthu inu mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa+ ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.”+

4 “Taonani! Tsiku loyaka ngati ng’anjo likubwera,+ ndipo anthu onse odzikuza ndi onse ochita zoipa adzakhala ngati mapesi.+ Tsiku limene likubweralo lidzawanyeketsa moti pa iwo sipadzatsala mizu kapena nthambi,”+ watero Yehova wa makamu. 2 “Koma inu amene mukuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani+ ndipo m’mapiko mwake mudzakhala mphamvu yochiritsa.+ Inu mudzanyamuka ndi kudumphadumpha ngati ana a ng’ombe amphongo onenepa.”+

3 “Anthu inu mudzapondaponda anthu oipa. Iwo adzakhala ngati fumbi kumapazi anu pa tsiku limene ndidzachitepo kanthu,”+ watero Yehova wa makamu.

4 “Anthu inu kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga. Kumbukirani malamulo ndi zigamulo zimene ndinam’patsa ku Horebe zokhudza Aisiraeli onse.+

5 “Tamverani anthu inu! Tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha lisanafike,+ ndidzakutumizirani mneneri Eliya.+ 6 Iye adzatembenuza mitima ya abambo kuti ikhale ngati ya ana, ndipo adzatembenuza mitima ya ana kuti ikhale ngati ya abambo.* Adzachita zimenezi kuti ine ndisabwere kudzawononga dziko lapansi.”+

(Malemba amene anawalemba m’Chiheberi ndi m’Chiaramu athera pamenepa. Malemba otsatirawa anawalemba m’Chigiriki)

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “amene ali maso ndiponso amene akuyankha.”

Mawu ake enieni, “mbewu ya Mulungu.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”

Mawu ake enieni, “Iye adzatembenuza mtima wa abambo kuubwezera kwa ana, ndi mtima wa ana kubwezera kwa abambo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena