Mateyu
1 Buku la mzere wa makolo+ a Yesu Khristu, mwana wa Davide,+ mwana wa Abulahamu:+
Isaki anabereka Yakobo.+
Yakobo anabereka Yuda+ ndi abale ake.
3 Yuda anabereka Perezi+ ndi Zera, ndipo mayi awo anali Tamara.
Perezi anabereka Hezironi.+
Hezironi anabereka Ramu.+
4 Ramu anabereka Aminadabu.
Aminadabu anabereka Naasoni.+
Naasoni anabereka Salimoni.+
5 Salimoni anabereka Boazi, ndipo mayi ake anali Rahabi.+
Boazi anabereka Obedi, ndipo mayi ake anali Rute.+
Obedi anabereka Jese.+
Davide anabereka Solomo,+ yemwe mayi ake anali mkazi wa Uriya.
7 Solomo anabereka Rehobowamu.+
Rehobowamu anabereka Abiya.
Yehosafati anabereka Yehoramu.+
Yehoramu anabereka Uziya.
Yotamu anabereka Ahazi.+
Ahazi anabereka Hezekiya.+
10 Hezekiya anabereka Manase.+
Amoni+ anabereka Yosiya.
11 Yosiya+ anabereka Yekoniya+ ndi abale ake pa nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo.+
12 Ayuda atatengedwa kupita ku Babulo, Yekoniya anabereka Salatiyeli.+
Salatiyeli anabereka Zerubabele.+
13 Zerubabele anabereka Abiyudi.
Abiyudi anabereka Eliyakimu.
Eliyakimu anabereka Azoro.
14 Azoro anabereka Zadoki.
Zadoki anabereka Akimu.
Akimu anabereka Eliyudi.
15 Eliyudi anabereka Eleazara.
Eleazara anabereka Matani.
Matani anabereka Yakobo.
16 Yakobo anabereka Yosefe mwamuna wake wa Mariya, amene anabereka Yesu,+ wotchedwa Khristu.+
17 Chotero, mibadwo yonse kuchokera pa Abulahamu kukafika pa Davide inalipo mibadwo 14, ndipo kuchokera pa Davide kukafika nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo panali mibadwo 14. Kuchokera pa nthawi imene Ayudawo anatengedwa kupita ku Babulo kukafika pa Khristu, panali mibadwo 14.
18 Koma kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Pa nthawi imene mayi ake Mariya anali atalonjezedwa+ ndi Yosefe kuti adzam’kwatira, Mariyayo anapezeka kuti ali ndi pakati mwa mzimu woyera+ asanatengane. 19 Koma mwamuna wake Yosefe, pokhala munthu wolungama ndiponso posafuna kumuchititsa manyazi kwa anthu,+ anaganiza zomusiya+ mwamseri.* 20 Koma ataganiza mozama za nkhani imeneyi, mngelo wa Yehova* anamuonekera m’maloto n’kumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutengera Mariya mkazi wako kunyumba, chifukwa chakuti pakati alinapopa pachitika mwa mphamvu ya mzimu woyera.+ 21 Iye adzabereka mwana wamwamuna, ndipo dzina lake udzamutche Yesu,*+ chifukwa adzapulumutsa+ anthu ake+ ku machimo awo.”+ 22 Zonsezi zinachitika kuti zimene Yehova ananena kudzera mwa mneneri+ wake zikwaniritsidwe.+ Iye anati: 23 “Tamverani! Namwali+ adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli,”+ lotanthauza “Mulungu Ali Nafe,”+ likamasuliridwa.
24 Ndiyeno Yosefe anadzuka ndi kuchita mmene mngelo wa Yehova anamulangizira. Anatenga mkazi wake ndi kupita naye kunyumba. 25 Koma sanagone+ naye mpaka anabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo anamutcha dzina lakuti Yesu.+
2 Yesu atabadwa ku Betelehemu+ wa Yudeya m’masiku a mfumu Herode,*+ okhulupirira nyenyezi+ ochokera kumadera a kum’mawa anabwera ku Yerusalemu. 2 Iwo ananena kuti: “Ili kuti mfumu ya Ayuda imene yabadwa?+ Chifukwa pamene tinali kum’mawa, tinaona nyenyezi+ yake ndipo tabwera kudzaigwadira.” 3 Mfumu Herode itamva zimenezi, inavutika mumtima limodzi ndi Yerusalemu yense. 4 Choncho Herode anasonkhanitsa ansembe onse aakulu ndi alembi a anthu, ndipo anayamba kuwafunsa za kumene Khristu adzabadwire. 5 Iwo anamuyankha kuti: “Adzabadwira ku Betelehemu+ wa Yudeya, pakuti kudzera mwa mneneri zimenezi zinalembedwa motere, 6 ‘Iwe Betelehemu+ wa m’dziko la Yuda, suli mzinda waung’ono kwambiri kwa olamulira a Yuda, chifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulira+ amene adzaweta+ anthu anga, Aisiraeli.’”
7 Kenako, Herode anaitanitsa mwamseri okhulupirira nyenyezi aja, ndipo atawafunsa mosamala, anadziwa nthawi yeniyeni imene nyenyeziyo inaonekera. 8 Ndiyeno powatumiza ku Betelehemu, iye anawauza kuti: “Pitani mukam’funefune mwanayo mosamala, ndipo mukakam’peza mudzandidziwitse, kuti nanenso ndipite kukam’gwadira.”+ 9 Atamva zimene mfumu inanena, anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali kum’mawa+ ija inawatsogolera, mpaka inakaima m’mwamba pamalo pamene panali mwanayo. 10 Ataona kuti nyenyeziyo yaima anakondwera kwambiri. 11 Tsopano atalowa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya. Choncho anagwada ndi kumuweramira. Kenako anamasula chuma chawo ndi kupereka kwa mwanayo mphatso za golide, lubani ndi mule. 12 Koma chifukwa chakuti analandira chenjezo la Mulungu+ m’maloto kuti asapitenso kwa Herode, iwo anabwerera kudziko lakwawo kudzera njira ina.
13 Okhulupirira nyenyezi aja atachoka, mngelo wa Yehova+ anaonekera kwa Yosefe m’maloto n’kumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo. Ukakhale kumeneko kufikira nthawi imene ndidzakuuze, chifukwa Herode akukonza zoyamba kufunafuna mwanayu kuti amuphe.” 14 Chotero Yosefe anadzuka usiku n’kutenga mwana uja limodzi ndi mayi ake. Anachoka kumeneko kupita ku Iguputo, 15 ndipo anakhala kumeneko mpaka kumwalira kwa Herode, kuti zimene Yehova analankhula kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe.+ Iye anati: “Ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.”+
16 Koma Herode, poona kuti okhulupirira nyenyezi aja am’pusitsa, anakwiya koopsa. Choncho anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna m’Betelehemu ndi m’zigawo zake zonse, kuyambira azaka ziwiri kutsika m’munsi, mogwirizana ndi nthawi imene anafunsira mosamala kwa okhulupirira nyenyezi aja.+ 17 Zimenezi zinakwaniritsa mawu onenedwa kudzera mwa mneneri Yeremiya, akuti: 18 “Mawu anamveka ku Rama,+ kulira ndi kubuma mofuula. Anali Rakele+ kulirira ana ake ndipo sanamve kumutonthoza, chifukwa ana akewo kunalibenso.”
19 Herode atamwalira, mngelo wa Yehova anaonekera kwa Yosefe m’maloto+ ku Iguputo 20 ndipo anamuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo upite m’dziko la Isiraeli, chifukwa amene anali kufuna moyo wa mwanayu anafa.” 21 Chotero Yosefe ananyamuka n’kutenga mwanayo ndi mayi ake n’kukalowa m’dziko la Isiraeli. 22 Koma atamva kuti Arikelao ndi amene akulamulira monga mfumu ya Yudeya m’malo mwa bambo ake Herode, anachita mantha kupita kumeneko. Komanso, chifukwa chakuti analandira chenjezo la Mulungu m’maloto,+ iwo anapita m’dera la Galileya.+ 23 Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritsidwe mawu onenedwa kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”+
3 M’masiku amenewo, Yohane M’batizi+ anapita m’chipululu+ cha Yudeya n’kuyamba kulalikira. 2 Iye anali kulalikira kuti: “Lapani,+ pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.”+ 3 Mneneri Yesaya ananenera za iyeyu+ m’mawu awa: “Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti, ‘Konzani+ njira ya Yehova anthu inu! Wongolani misewu yake.’” 4 Koma Yohane ameneyu, anali kuvala chovala chaubweya wa ngamila+ ndi lamba wachikopa+ m’chiuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe+ ndi uchi.+ 5 Choncho anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndiponso ochokera m’midzi yonse yapafupi ndi Yorodano anali kubwera kwa iye. 6 Iye anali kuwabatiza mumtsinje wa Yorodano,+ ndipo anthuwo anali kuulula machimo awo poyera.
7 Pamene Yohane anaona Afarisi ndi Asaduki+ ambiri akubwera ku ubatizowo, anawauza kuti: “Ana a njoka inu,+ ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+ 8 Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kulapa.+ 9 Musamadzinyenge kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’+ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu angathe kuutsira Abulahamu+ ana kuchokera kumiyala iyi. 10 Nkhwangwa+ yaikidwa kale pamizu yamitengo. Chotero mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa+ ndi kuponyedwa pamoto.+ 11 Inetu ndikukubatizani m’madzi+ chifukwa cha kulapa kwanu,+ koma amene akubwera+ m’mbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake.+ Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyera+ komanso ndi moto.+ 12 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili m’manja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira m’nkhokwe,+ koma mankhusu adzawatentha+ ndi moto umene sungazimitsidwe.”
13 Kenako Yesu anabwera kwa Yohane ku Yorodano kuchokera ku Galileya,+ kuti iye amubatize.+ 14 Koma Yohane anayesa kumuletsa ponena kuti: “Ine ndiye wofunika kubatizidwa ndi inu, nanga inu mukubweranso kwa ine kodi?” 15 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Pa nthawi ino lola kuti zikhale choncho, chifukwa n’koyenera kwa ife kutero kuti tikwaniritse chilungamo chonse.”+ Atatero, anasiya kumuletsa. 16 Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka,+ ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda+ kudzamutera.+ 17 Panamvekanso mawu+ ochokera kumwamba onena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga+ wokondedwa,+ amene ndimakondwera naye.”+
4 Kenako mzimu unatsogolera Yesu kuchipululu+ kuti akayesedwe+ ndi Mdyerekezi. 2 Atasala kudya masiku 40 usana ndi usiku,+ anamva njala. 3 Ndiyeno Woyesayo+ anabwera n’kumuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu,+ uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.” 4 Koma poyankha iye anati: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.’”*+
5 Kenako Mdyerekezi anamutenga ndi kupita naye mumzinda woyera,+ ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi 6 n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi,+ pajatu Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu, ndipo adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala uliwonse.’”+ 7 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amatinso, ‘Usamuyese Yehova Mulungu wako.’”+
8 Ndiyeno Mdyerekezi anamutenganso ndi kupita naye paphiri lalitali kwambiri, ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko+ ndi ulemerero wawo. 9 Kenako anamuuza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi+ ngati mutangogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.”+ 10 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira,+ ndipo uyenera kutumikira+ iye yekha basi.’”+ 11 Pamenepo Mdyerekezi uja anamusiya,+ ndipo kunabwera angelo ndi kuyamba kum’tumikira.+
12 Tsopano Yesu atamva kuti Yohane amugwira,+ anachoka kumeneko ndipo anapita ku Galileya.+ 13 Komanso atachoka ku Nazareti, anafika ku Kaperenao+ n’kupeza malo okhala m’mphepete mwa nyanja m’zigawo za Zebuloni ndi Nafitali,+ 14 kuti mawu amene ananenedwa kudzera mwa Yesaya mneneri akwaniritsidwe. Iye ananena kuti: 15 “Anthu okhala m’dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, m’mbali mwa msewu wa kunyanja kutsidya lina la Yorodano, ku Galileya+ kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina, 16 anthu okhala mu mdima+ anaona kuwala kwakukulu,+ ndipo anthu okhala m’dera la mthunzi wa imfa, kuwala+ kunawatulukira.”+ 17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira ndi kunena kuti: “Lapani+ anthu inu, pakuti ufumu+ wakumwamba wayandikira.”
18 Pamene anali kuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona amuna awiri apachibale akuponya ukonde wophera nsomba m’nyanja, pakuti anali asodzi. Mayina awo anali Simoni+ wotchedwa Petulo+ ndi Andireya. 19 Iye anawauza kuti: “Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 20 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo+ n’kumutsatira. 21 Atapitirira pamenepo, anaona amuna enanso awiri+ apachibale, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi m’bale wake Yohane. Iwo anali m’ngalawa limodzi ndi bambo awo, a Zebedayo,+ akusoka maukonde awo, ndipo anawaitana. 22 Nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo awo n’kumutsatira.
23 Atatero, anayendayenda+ m’Galileya+ yense kuphunzitsa m’masunagoge+ mwawo, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa anthu matenda amtundu uliwonse+ ndi zofooka zilizonse. 24 Choncho mbiri yake inafalikira mu Siriya+ monse. Anthu anamubweretsera onse amene sanali kumva bwino m’thupi,+ amene anali kuvutika ndi matenda komanso zowawa zamitundumitundu, ogwidwa ndi ziwanda, akhunyu,+ ndi anthu akufa ziwalo, ndipo iye anawachiritsa. 25 Chotero makamu a anthu ambiri ochokera ku Galileya,+ ku Dekapole, ku Yerusalemu,+ ku Yudeya komanso ochokera kutsidya lina la Yorodano, anam’tsatira.
5 Ataona khamu la anthu, anakwera m’phiri. Atakhala pansi, ophunzira ake anabwera kwa iye. 2 Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:
3 “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu,+ chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.+
4 “Odala ndi anthu amene akumva chisoni, chifukwa adzasangalatsidwa.+
5 “Odala ndi anthu amene ali ofatsa,+ chifukwa adzalandira dziko lapansi.+
6 “Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu+ la chilungamo, chifukwa adzakhuta.+
7 “Odala ndi anthu achifundo,+ chifukwa adzachitiridwa chifundo.
8 “Odala ndi anthu oyera mtima,+ chifukwa adzaona Mulungu.+
9 “Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere,+ chifukwa adzatchedwa ‘ana+ a Mulungu.’
10 “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa+ chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.
11 “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani+ ndi kukuzunzani,+ komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. 12 Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe,+ chifukwa mphoto+ yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri+ amene analipo inu musanakhaleko.
13 “Inu ndinu mchere+ wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yake angaibwezeretse motani? Sungagwire ntchito iliyonse koma ungafunike kuutaya kunja+ kumene anthu akaupondaponda.
14 “Inu ndinu kuwala kwa dziko.+ Mzinda ukakhala paphiri subisika. 15 Anthu akayatsa nyale, saivundikira ndi dengu,+ koma amaiika pachoikapo nyale ndipo imaunikira onse m’nyumbamo. 16 Momwemonso, onetsani kuwala+ kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino+ ndi kuti alemekeze+ Atate wanu wakumwamba.
17 “Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo+ kapena Zolemba za aneneri. Sindinabwere kudzaziwononga koma kudzazikwaniritsa.+ 18 Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta,+ kusiyana n’kuti kalemba kochepetsetsa kapena kachigawo kamodzi ka lemba kachoke m’Chilamulo zinthu zonse zisanachitike.+ 19 Chotero aliyense wophwanya+ lililonse la malamulo aang’ono awa ndi kuphunzitsa anthu kuphwanya malamulowo, adzakhala ‘wosayenera kulowa’ mu ufumu wakumwamba.+ Koma aliyense wotsatira ndi kuphunzitsa malamulowa,+ ameneyo adzakhala ‘woyenera kulowa’+ mu ufumu wakumwamba. 20 Pakuti ndikukuuzani inu kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha alembi ndi Afarisi,+ ndithudi simudzalowa+ mu ufumu wakumwamba.
21 “Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti ‘Usaphe munthu.+ Aliyense amene wapha mnzake+ wapalamula mlandu wa kukhoti.’+ 22 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ m’bale wake wapalamula mlandu+ wa kukhoti. Komano aliyense wonenera m’bale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe!’ adzapita ku Gehena* wamoto.+
23 “Choncho ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe,+ ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa,+ 24 siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba,+ ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.+
25 “Thetsa nkhani mofulumira ndi munthu wokuimba mlandu pamene ukupita naye kukhoti, kuti mwina wokuimba mlanduyo+ asakakupereke kwa woweruza. Komanso kuti woweruzayo asakakupereke kwa msilikali wa pakhoti kuti akuponye m’ndende. 26 Kunena zoona, sudzatulukamo kufikira utalipira kakhobidi kotsirizira.+
27 “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’+ 28 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi+ mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo+ mumtima mwake.+ 29 Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa,* ulikolowole ndi kulitaya.+ Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe+ m’Gehena. 30 Komanso ngati dzanja lako lamanja limakuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya.+ Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe m’Gehena.
31 “Pajanso anati, ‘Aliyense wothetsa ukwati+ ndi mkazi wake, apatse mkaziyo kalata yothetsera ukwati.’+ 32 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wothetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha dama,*+ amamuchititsa chigololo akakwatiwanso,+ ndipo aliyense wokwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.+
33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+ 34 Koma ine ndikukuuzani kuti: Usamalumbire+ n’komwe, kutchula kumwamba, chifukwa ndi kumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu,+ 35 kapena kutchula dziko lapansi chifukwa ndi chopondapo mapazi ake,+ kapena kutchula Yerusalemu chifukwa ndi mzinda+ wa Mfumu yaikulu. 36 Kapena usalumbire kutchula mutu wako, chifukwa sungathe kusandutsa ngakhale tsitsi limodzi kukhala loyera kapena lakuda. 37 Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi,+ pakuti mawu owonjezera pamenepa achokera kwa woipayo.+
38 “Inu munamva kuti anati, ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’+ 39 Koma ine ndikukuuzani kuti: Usalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja,+ umutembenuzirenso linalo. 40 Ngati munthu akufuna kukutengera kukhoti kuti akulande malaya ako amkati, m’patsenso akunja.+ 41 Winawake waudindo akakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire mtunda wa makilomita awiri.+ 42 Munthu akakupempha kanthu m’patse, ndipo munthu wofuna kukongola kanthu kwa iwe popanda chiwongoladzanja usamukanize.+
43 “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako+ ndi kudana ndi mdani wako.’+ 44 Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kupempherera amene akukuzunzani,+ 45 kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+ 46 Pakuti mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandira mphoto yotani?+ Kodi okhometsa msonkho sachitanso zimenezo? 47 Ngati mupatsa moni abale anu okha, kodi n’chiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo? 48 Choncho khalani angwiro, monga mmene Atate wanu wakumwamba alili wangwiro.+
6 “Samalani kuti musamachite chilungamo chanu+ pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni, chifukwa mukatero simudzalandira mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba. 2 Chotero pamene ukupereka mphatso zachifundo,+ usalize lipenga+ muja amachitira onyenga m’masunagoge ndi m’misewu, kuti anthu awatamande. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 3 Koma iwe, pamene ukupereka mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita, 4 kuti mphatso zako zachifundo zikhale zamseri. Ukatero Atate wako amene akuyang’ana kuseriko adzakubwezera.+
5 “Komanso pamene mukupemphera, musamachite ngati anthu onyenga. Pakuti iwo amakonda kuimirira+ m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona.+ Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha+ ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka.+ Ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera. 7 Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza+ ngati mmene amachitira anthu a mitundu ina, chifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu awamvera akanena mawu ambirimbiri. 8 Chotero inu musafanane nawo, chifukwa Mulungu Atate wanu amadziwa zimene mukufuna+ musanapemphe n’komwe.
9 “Koma inu muzipemphera motere:+
“‘Atate wathu wakumwamba, dzina+ lanu liyeretsedwe.+ 10 Ufumu+ wanu ubwere. Chifuniro chanu+ chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.+ 11 Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.+ 12 Mutikhululukire zolakwa* zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira.*+ 13 Musatilowetse m’mayesero,+ koma mutilanditse kwa woipayo.’+
14 “Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani.+ 15 Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.+
16 “Pamene mukusala kudya,+ lekani kumaonetsa nkhope yachisoni ngati mmene onyenga aja amachitira. Iwo amaipitsa nkhope zawo kuti aonekere kwa anthu kuti akusala kudya.+ Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 17 Koma iwe, pamene ukusala kudya, dzola mafuta m’mutu mwako ndi kusamba nkhope yako,+ 18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya, koma kwa Atate wako amene ali kosaoneka.+ Ukatero Atate wako amene akukuona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.
19 “Lekani kudziunjikira chuma+ padziko lapansi, pamene njenjete* ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. 20 Koma unjikani chuma chanu kumwamba,+ kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge,+ ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba. 21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.
22 “Nyale ya thupi ndi diso.+ Chotero ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala. 23 Koma ngati diso lako lili loipa,+ thupi lako lonse lidzachita mdima. Choncho ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima, ndiye kuti mdimawo ndi wandiweyani!+
24 “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo,+ kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.+
25 “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Lekani kudera nkhawa+ moyo wanu kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapenanso kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo suposa chakudya, ndipo kodi thupi siliposa chovala?+ 26 Onetsetsani mbalame+ zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?+ 27 Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa?+ 28 Komanso pa nkhani ya zovala, n’chifukwa chiyani mukuda nkhawa? Phunzirani pa mmene maluwa+ akutchire amakulira. Sagwira ntchito, ndiponso sawomba nsalu. 29 Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo+ mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. 30 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkheza pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu?+ 31 Choncho musamade nkhawa+ n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ 32 Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.+
33 “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake,+ ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.+ 34 Musamade nkhawa za tsiku lotsatira,+ chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.
7 “Lekani kuweruza ena+ kuti inunso musaweruzidwe, 2 pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho.+ Ndipo muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.+ 3 Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga* la nyumba umene uli m’diso lako?+ 4 Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga la nyumba?+ 5 Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwino mmene ungachotsere kachitsotso m’diso la m’bale wako.
6 “Musamapatse agalu zinthu zopatulika,+ kapena kuponyera nkhumba ngale zanu, kuopera kuti zingapondeponde ngalezo+ kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.
7 “Pemphanibe,+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe,+ ndipo adzakutsegulirani. 8 Pakuti aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira. 9 Inde, ndani pakati panu amene mwana wake+ atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? 10 Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11 Chotero ngati inuyo, ngakhale kuti ndinu oipa,+ mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino+ kwa onse om’pempha!
12 “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni,+ inunso muwachitire zomwezo, pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.+
13 “Lowani pachipata chopapatiza.+ Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. 14 Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.+
15 “Chenjerani ndi aneneri onyenga+ amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa,+ koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.+ 16 Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.+ Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamitula, amatero kodi?+ 17 Momwemonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.+ 18 Mtengo wabwino sungabale zipatso zopanda pake, ndiponso mtengo wovunda sungabale zipatso zabwino. 19 Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino amaudula ndi kuuponya pamoto.+ 20 Chotero anthu amenewo mudzawazindikira ndi zipatso zawo.+
21 “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita+ chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.+ 22 Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye,+ kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’+ 23 Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: Sindikukudziwani ngakhale pang’ono!+ Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.+
24 “Chotero aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.+ 25 Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo. 26 Aliyense wakumva mawu angawa koma osawachita+ adzafanizidwa ndi munthu wopusa+ amene anamanga nyumba yake pamchenga. 27 Ndiye kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo+ moti inagwa, ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”+
28 Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa+ ndi kaphunzitsidwe kake, 29 chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamuliro,+ osati monga alembi awo.
8 Atatsika m’phirimo, chikhamu cha anthu chinam’tsatira. 2 Kenako panafika munthu wakhate.+ Munthuyo anamugwadira n’kunena kuti: “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” 3 Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Ndikufuna. Khala woyera.”+ Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+ 4 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi,+ koma upite ukadzionetse kwa wansembe,+ ndipo ukapereke mphatso+ imene Mose analamula, kuti ikhale umboni kwa iwo.”
5 Atalowa mumzinda wa Kaperenao,+ kapitawo wa asilikali anabwera kwa iye ndi kum’pempha 6 kuti: “Ambuye, wantchito wanga wafa ziwalo moti ali gone m’nyumba, ndipo akuzunzika koopsa.” 7 Iye anamuyankha kuti: “Ndikafika kumeneko ndikam’chiritsa.” 8 Poyankha, kapitawo wa asilikali uja anati: “Ambuye, sindine munthu woyenera kuti inu mukalowe m’nyumba mwanga, koma mungonena mawu okha ndipo wantchito wangayo achira. 9 Pakuti inenso ndili ndi akuluakulu ondiyang’anira, komanso ndili ndi asilikali amene ali pansi panga. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’+ amapita, wina ndikamuuza kuti ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.” 10 Atamva zimenezo, Yesu anadabwa ndipo anauza amene anali kum’tsatira aja kuti: “Kunena zoona, mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.+ 11 Koma ndikukutsimikizirani kuti ambiri ochokera kum’mawa ndi kumadzulo+ adzabwera ndi kukhala patebulo limodzi ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo mu ufumu+ wakumwamba,+ 12 pamene ana a ufumuwo+ adzaponyedwa kunja kumdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”+ 13 Kenako Yesu anauza kapitawo wa asilikaliyo kuti: “Pita. Malinga ndi chikhulupiriro chako, chimene ukufuna chichitike.”+ Mu ola lomwelo, wantchito uja anachira.
14 Tsopano Yesu, atalowa m’nyumba mwa Petulo, anaona apongozi aakazi a Petulo+ ali gone, akudwala malungo.*+ 15 Choncho anagwira dzanja la mayiwo,+ ndipo malungowo anatheratu, moti anadzuka n’kuyamba kumutumikira.+ 16 Koma chakumadzulo, anthu anamubweretsera anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda, ndipo iye anatulutsa mizimu imeneyo ndi mawu okha. Onse amene sanali kumva bwino m’thupi anawachiritsa. 17 Anachita izi kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: “Iye anatenga matenda athu n’kunyamula zowawa zathu.”+
18 Pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lamuzungulira, analangiza ophunzira ake kuti akankhire ngalawa pamadzi n’kupita kutsidya lina.+ 19 Tsopano kunabwera mlembi wina ndi kumuuza kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.”+ 20 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.”+ 21 Kenako wina mwa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.” 22 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Iwe unditsatirebe ine, ndipo aleke akufa aike akufa awo.”+
23 Ndiyeno pamene analowa m’ngalawa,+ ophunzira ake anam’tsatira. 24 Kenako panyanjapo panabuka mphepo yamphamvu moti mafunde anali kulowa m’ngalawamo, koma iye anali m’tulo.+ 25 Ndipo iwo anapita kukam’dzutsa+ kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” 26 Koma iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”+ Kenako anadzuka n’kudzudzula mphepo ndi nyanjayo, ndipo panachita bata lalikulu.+ 27 Chotero amunawo anadabwa n’kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi wotani,+ moti ngakhale mphepo ndi nyanja zikum’mvera?”
28 Atafika kutsidya linalo, m’dera la Agadara,+ anakumana ndi amuna awiri ogwidwa ndi ziwanda+ akuchokera m’manda achikumbutso. Amunawa anali ochititsa mantha nthawi zonse moti panalibe aliyense woyesa dala kudutsa msewu umenewo. 29 Nthawi yomweyo iwo anafuula, kuti: “Kodi tili nanu chiyani, Mwana wa Mulungu?+ Kodi mwabwera kudzatizunza+ nthawi yoikidwiratu isanakwane?”+ 30 Koma pamtunda wautali ndithu kuchokera pamenepo, nkhumba zambiri zinali kudya. 31 Chotero ziwandazo zinayamba kum’chonderera kuti: “Ngati mukufuna kutitulutsa, mutitumize munkhumbazi.”+ 32 Pamenepo iye anaziuza kuti: “Pitani!” Choncho zinatuluka ndi kukalowa m’nkhumba zija. Nthawi yomweyo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi ndi kulumphira m’nyanja, ndipo zinafera m’madzimo.+ 33 Koma amene anali kuyang’anira ziwetozo anathawa ndipo atalowa mumzinda anafotokoza zonse kuphatikizapo zimene zinachitikira amuna ogwidwa ndi ziwanda aja. 34 Zitatero, anthu onse mumzindawo anapita kukakumana ndi Yesu. Atamuona, anam’pempha kuti achoke m’madera akwawoko.+
9 Chotero Yesu anakwera ngalawa n’kuwolokera tsidya lina, ndipo anapita kumzinda umene anali kukhala.+ 2 Kumeneko anthu anam’bweretsera munthu wakufa ziwalo, atagona pakabedi.+ Poona chikhulupiriro chawo, Yesu anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Limba mtima, mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+ 3 Atatero, alembi ena anang’ung’udza chamumtima kuti: “Munthu ameneyu akunyoza Mulungu.”+ 4 Koma Yesu, podziwa zimene iwo anali kuganiza,+ ananena kuti: “N’chifukwa chiyani mukuganiza zinthu zoipa m’mitima mwanu?+ 5 Mwachitsanzo, chapafupi n’chiti, kunena kuti, Machimo ako akhululukidwa, kapena kunena kuti, Nyamuka uyende?+ 6 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo+ . . .” pamenepo anauza wakufa ziwalo uja kuti: “Nyamuka, tenga kabedi kakoka uzipita kwanu.”+ 7 Ndipo ananyamuka n’kupita kwawo. 8 Khamu la anthulo litaona zimenezi, linagwidwa ndi mantha ndipo linatamanda Mulungu,+ amene anapereka mphamvu zimenezo+ kwa anthu.
9 Atachoka pamenepo, Yesu anaona munthu wina wotchedwa Mateyu atakhala pansi mu ofesi yokhomera msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ Nthawi yomweyo ananyamuka ndi kum’tsatira.+ 10 Nthawi inayake, pamene anali kudya patebulo m’nyumba ina,+ kunabwera okhometsa msonkho ndi ochimwa ambiri ndipo anayamba kudya pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11 Koma poona zimenezi, Afarisi anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?”+ 12 Iye atamva zimenezo, anayankha kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala,+ koma odwala ndi amene amamufuna. 13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”
14 Kenako ophunzira a Yohane anabwera kwa iye n’kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 15 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo+ ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa+ pakati pawo, ndipo pa nthawiyo adzasala kudya.+ 16 Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Pakuti mphamvu yonse ya chigambacho ingakoke ndi kung’amba malayawo ndipo kung’ambikako kungawonjezeke kwambiri.+ 17 Ndiponso anthu sathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Akachita zimenezo, matumba achikopawo amaphulika ndipo vinyoyo amatayika moti matumbawo amawonongeka.+ Koma anthu amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa atsopano, ndipo zonse ziwirizo zimasungika bwino.”+
18 Pamene anali kuwauza zimenezi, wolamulira wina+ anam’yandikira. Kenako anamugwadira+ n’kunena kuti: “Panopa mwana wanga wamkazi ayenera kuti wamwalira kale.+ Koma tiyeni mukamukhudze ndi dzanja lanu ndipo akhala ndi moyo.”+
19 Pamenepo Yesu ananyamuka ndi kumutsatira. Ophunzira ake anachitanso chimodzimodzi. 20 Tsopano mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi kwa zaka 12+ anafika kumbuyo kwake n’kugwira ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake akunja,+ 21 chifukwa mumtima mwake anali kunena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”+ 22 Yesu anatembenuka, ndipo anaona mayiyo n’kunena kuti: “Mwanawe, limba mtima, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Kuchokera pa ola limenelo mayiyo anachira.+
23 Tsopano atalowa m’nyumba ya wolamulira uja,+ anaona oliza zitoliro komanso khamu la anthu likubuma.+ 24 Yesu anawauza kuti: “Tulukani muno, pakuti mtsikanayu sanamwalire ayi, koma akugona.”+ Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kum’seka monyodola.+ 25 Atatulutsa anthu aja panja, iye analowa ndi kugwira dzanja la mtsikanayo,+ ndipo iye anadzuka.+ 26 Nkhani imeneyi inamveka m’dera lonselo.
27 Pamene Yesu anali kudutsa kuchokera kumeneko, anthu awiri akhungu+ anam’tsatira. Iwo anafuula ndi kunena kuti: “Mutichitire chifundo,+ Mwana wa Davide.” 28 Yesu atalowa m’nyumba, anthu akhunguwo anabwera kwa iye, ndipo anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chikhulupiriro+ kuti ndingachite zimenezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde, Ambuye.” 29 Kenako anawagwira m’maso,+ n’kunena kuti: “Malinga ndi chikhulupiriro chanu zichitike momwemo kwa inu,” 30 ndipo maso awo anatseguka. Chotero Yesu anawalamula mwamphamvu kuti: “Samalani, aliyense asadziwe zimenezi.”+ 31 Koma iwo, atatuluka kunja, anafalitsa za iye ponseponse m’dera limenelo.+
32 Tsopano pamene iwo anali kunyamuka, anthu anam’bweretsera munthu wosalankhula wogwidwa ndi chiwanda.+ 33 Atatulutsa chiwandacho, munthu wosalankhulayo analankhula,+ moti khamu la anthulo linadabwa+ ndipo linanena kuti: “Zinthu zoterezi sizinaonekepo n’kale lonse mu Isiraeli.” 34 Koma Afarisi anayamba kunena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+
35 Tsopano Yesu anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.+ 36 Poona chikhamu cha anthu, iye anawamvera chisoni,+ chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.+ 37 Pamenepo anauza ophunzira ake kuti: “Inde, zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.+ 38 Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.”+
10 Chotero anaitana ophunzira ake 12 aja ndi kuwapatsa ulamuliro pa mizimu yonyansa,+ kuti athe kuitulutsa ndi kuchiritsa matenda a mtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.
2 Mayina a atumwi 12+ aja ndi awa:+ Simoni, wotchedwa Petulo,*+ ndi Andireya+ m’bale wake. Yakobo mwana wa Zebedayo+ ndi m’bale wake Yohane. 3 Filipo ndi Batolomeyo,+ Tomasi+ ndi Mateyu+ wokhometsa msonkho, Yakobo mwana wa Alifeyo,+ Tadeyo, 4 Simoni Kananiya,*+ ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anapereka+ Yesu.
5 Yesu anatumiza atumwi 12 amenewa, ndipo anawapatsa malangizo awa:+ “Musapite mumsewu wa anthu a mitundu ina, ndipo musalowe mumzinda wa Asamariya.+ 6 M’malomwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosochera za nyumba ya Isiraeli.+ 7 Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’+ 8 Chiritsani odwala,+ ukitsani anthu akufa, yeretsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.+ 9 Musatenge golide, siliva kapena mkuwa m’zikwama zanu za ndalama.+ 10 Musatenge thumba la chakudya cha pa ulendo, kapena malaya awiri amkati, nsapato kapena ndodo, chifukwa wantchito ayenera kulandira chakudya chake.+
11 “Mukalowa mumzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera, ndipo mukhalebe momwemo kufikira nthawi yochoka.+ 12 Pamene mukulowa m’nyumba, perekani moni kwa a m’banja limenelo. 13 Ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere umene mukuifunira ukhale panyumbayo,+ koma ngati si yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Kulikonse kumene munthu sakakulandirani kapena kumvetsera mawu anu, potuluka m’nyumba imeneyo kapena mumzinda umenewo sansani fumbi kumapazi anu.+ 15 Ndithu ndikukuuzani, Chilango cha Sodomu+ ndi Gomora pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha mzinda umenewo.+
16 “Taonani! Ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu.+ Chotero khalani ochenjera ngati njoka+ koma oona mtima ngati nkhunda.+ 17 Chenjerani ndi anthu,+ pakuti adzakuperekani kumakhoti aang’ono,+ ndipo adzakukwapulani+ m’masunagoge awo.+ 18 Inde, adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu+ chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni+ kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina. 19 Koma akakuperekani kumeneko, musade nkhawa za mmene mukalankhulire kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule,+ 20 pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.+ 21 Komanso munthu adzapereka m’bale+ wake ku imfa, ndipo bambo adzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo awo ndipo adzawaphetsa.+ 22 Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa,+ koma yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.+ 23 Akakuzunzani mumzinda wina, muthawire mumzinda wina,+ pakuti ndithu ndikukuuzani, simudzamaliza kuzungulira+ mizinda yonse ya Isiraeli Mwana wa munthu asanafike.+
24 “Wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo kapolo saposa mbuye wake.+ 25 Wophunzira amangofanana ndi mphunzitsi wake, ndipo kapolo amangofanana ndi mbuye wake.+ Ngati anthu atchula mwininyumba kuti Belezebule,*+ kuli bwanji ena a m’banja lakelo, kodi sadzawanena zoposa pamenepa? 26 Choncho musawaope, pakuti palibe chobisika chimene sichidzaululika, ndipo palibe chinsinsi chimene sichidzadziwika.+ 27 Zimene ndimakuuzani mu mdima, muzinene poyera, ndipo zimene mumamva anthu akunong’onezana, muzilalikire pamadenga.+ 28 Musachite mantha+ ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo, m’malomwake, muziopa iye+ amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.*+ 29 Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu?+ Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.+ 30 Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga.+ 31 Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.+
32 “Chotero aliyense wovomereza pamaso pa anthu kuti ali kumbali yanga, inenso ndidzavomereza+ pamaso pa Atate wanga wakumwamba kuti ndili kumbali yake. 33 Koma aliyense wondikana ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamukana+ pamaso pa Atate wanga wakumwamba. 34 Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi, sindinabweretse mtendere+ koma lupanga. 35 Pakuti ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.+ 36 Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni. 37 Amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine sali woyenera ine. Komanso amene amakonda kwambiri mwana wake wamwamuna kapena wamkazi kuposa ine sali woyenera ine.+ 38 Ndiponso aliyense wosalandira mtengo wake wozunzikirapo* ndi kunditsatira sali woyenera ine.+ 39 Aliyense wopulumutsa moyo wake adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.+
40 “Amene wakulandirani walandiranso ine, ndipo amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ 41 Amene walandira mneneri chifukwa ndi mneneri adzalandira mphoto yofanana ndi imene mneneri amalandira,+ ndipo amene walandira munthu wolungama chifukwa ndi wolungama adzalandira mphoto yofanana ndi imene munthu wolungama amalandira.+ 42 Aliyense wopatsa mmodzi wa tiana iti ngakhale madzi ozizira okha m’kapu kuti amwe chifukwa ndi wophunzira, ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika ngakhale pang’ono.”+
11 Tsopano Yesu atamaliza kupereka malangizo kwa ophunzira ake 12 aja, anachoka kumeneko n’kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira kumizinda ina.+
2 Koma pamene Yohane anali m’ndende, anamva+ zimene Khristu anali kuchita, ndipo anatuma ophunzira ake 3 kukam’funsa kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?”+ 4 Poyankha Yesu ananena kuti: “Pitani mukamuuze Yohane zimene mukumva ndi kuona: 5 Akhungu akuonanso,+ olumala+ akuyendayenda, akhate+ akuyeretsedwa ndipo ogontha+ akumva. Akufa+ akuukitsidwa, ndipo kwa aumphawi uthenga wabwino ukulengezedwa.+ 6 Wodala amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.”+
7 Pamene ophunzira a Yohane anali kubwerera, Yesu anayamba kuuza khamu la anthulo za Yohane kuti: “Kodi munapita m’chipululu kukaona chiyani?+ Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+ 8 Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena? Iyayi, pajatu ovala zovala zapamwamba amapezeka m’nyumba za mafumu.+ 9 Nangano n’chifukwa chiyani munapita makamaka? Kukaona mneneri kapena? Inde, ndikukuuzani, woposadi mneneri.+ 10 Malemba amanena za iyeyu kuti, ‘Taona! Inetu ndikutumiza mthenga wanga choyamba, amene adzakukonzera njira!’+ 11 Ndithu ndikukuuzani anthu inu, Mwa onse obadwa kwa akazi,+ sanabadwepo wamkulu woposa Yohane M’batizi. Koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu+ wakumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu. 12 Kuyambira m’masiku a Yohane M’batizi mpaka tsopano anthu akulimbikira kupeza mwayi wolowa mu ufumu wakumwamba, ndipo amene akulimbikira mwakhama akuupeza.+ 13 Pakuti zonse, Zolemba za aneneri ndi Chilamulo, zinalosera mpaka nthawi ya Yohane.+ 14 Kaya mukhulupirira kapena ayi, Yohane ndiye ‘Eliya woyembekezeka kubwera uja.’+ 15 Amene ali ndi makutu amve.+
16 “Kodi m’badwo uwu ndiufanizire ndi ndani?+ Uli ngati ana aang’ono amene amakhala pansi m’misika n’kumafuulira anzawo osewera nawo+ 17 kuti, ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunadzigugude pachifuwa chifukwa cha chisoni.’+ 18 Mofanana ndi zimenezi, Yohane anabwera ndipo sanali kudya kapena kumwa.+ Koma anthu ankanena kuti, ‘Ali ndi chiwanda.’ 19 Kunabwera Mwana wa munthu ndipo anali kudya ndi kumwa,+ koma anthu akunenabe kuti, ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa.’+ Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.”+
20 Kenako anayamba kudzudzula mizinda imene anachitamo ntchito zambiri zamphamvu, chifukwa sinalape.+ 21 Iye anati: “Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida!+ chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu akanakhala atalapa kalekale, atavala ziguduli* ndi kukhala paphulusa.+ 22 Koma tsopano ndikukuuzani kuti, Chilango cha Turo ndi Sidoni pa Tsiku la Chiweruzo+ chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi chanu.+ 23 Iwenso Kaperenao,+ kodi udzakwezedwa kumwamba kapena? Ku Manda*+ n’kumene udzatsikira ndithu,+ chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Sodomu, mzindawo ukanakhala ulipobe mpaka lero. 24 Koma tsopano ndikukuuzani anthu inu kuti, Chilango cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha Kaperenao.”+
25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.+ 26 Inde Atate wanga, ndikukutamandani chifukwa inu munavomereza kuti zimenezi zichitike. 27 Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate+ okha, komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+ 28 Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa,+ ndipo ndidzakutsitsimutsani. 29 Senzani goli+ langa ndipo phunzirani kwa ine,+ chifukwa ndine wofatsa+ ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa,+ 30 pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”+
12 Pa nthawi ina, Yesu anali kudutsa m’munda wa tirigu pa tsiku la sabata.+ Ophunzira ake anamva njala ndipo anayamba kubudula ngala za tirigu n’kumadya.+ 2 Afarisi ataona zimenezi anamuuza kuti:+ “Taona! Ophunzira ako akuchita zosayenera kuzichita pa sabata.”+ 3 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita atamva njala pamodzi ndi amuna omwe anali naye?+ 4 Kodi sanalowe m’nyumba ya Mulungu ndi kudya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,+ umene iye ndi anthu omwe anali nawo aja sanayenera kudya malinga ndi malamulo,+ koma ansembe okha?+ 5 Kapena simunawerenge m’Chilamulo,+ kuti pa sabata ansembe m’kachisi anali kuchita zinthu mosalabadira kupatulika kwa tsiku la sabata koma anakhalabe osalakwa?+ 6 Koma ndikukuuzani kuti wamkulu kuposa kachisi+ ali pano. 7 Komabe, ngati mukanamvetsa tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo,+ osati nsembe,’+ simukanaweruza anthu osalakwa. 8 Pakuti Mwana wa munthu+ ndiye Mbuye wa sabata.”+
9 Atachoka malo amenewo, anakalowa m’sunagoge wawo. 10 Mmenemo munali munthu wopuwala dzanja.+ Chotero iwo anam’funsa kuti, “Kodi n’kololeka kuchiritsa odwala tsiku la sabata?” Cholinga chawo chinali kum’peza chifukwa, kuti amuzenge mlandu.+ 11 Koma iye anawayankha kuti: “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa imodzi, ndiyeno nkhosayo n’kugwera m’dzenje+ tsiku la sabata, sangaigwire ndi kuitulutsa?+ 12 Komatu munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa.+ Choncho, n’kololeka inde kuchita chinthu chabwino pa tsiku la sabata.” 13 Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhalanso bwinobwino ngati linzake.+ 14 Koma Afarisiwo anatuluka ndi kukakonza chiwembu choti amuphe.+ 15 Atadziwa zimenezi, Yesu anatuluka mmenemo. Anthu ambiri anam’tsatira ndipo iye anawachiritsa onsewo,+ 16 koma anawalamula mwamphamvu kuti asamuulule.+ 17 Anatero kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti:
18 “Taonani mtumiki wanga+ amene ndamusankha, wokondedwa wanga,+ amene moyo wanga ukukondwera naye. Ndidzaika mzimu wanga pa iye,+ ndipo adzasonyeza bwinobwino chilungamo chenicheni kwa anthu a mitundu ina. 19 Sadzakangana ndi munthu,+ kapena kufuula, ndipo palibe amene adzamva mawu ake m’misewu. 20 Bango lophwanyika sadzalisansantha ndipo nyale yofuka sadzaizimitsa,+ kufikira atakwanitsa kubweretsa chilungamo.+ 21 Ndithudi, m’dzina lake mitundu ya anthu idzayembekezera zabwino.”+
22 Pambuyo pake anam’bweretsera munthu wogwidwa chiwanda, amenenso anali wakhungu ndi wosalankhula, ndipo iye anam’chiritsa, moti munthuyo analankhula ndiponso anaona. 23 Zitatero, khamu la anthulo linadabwa kwambiri n’kunena kuti:+ “Kodi ameneyu sangakhale Mwana wa Davide uja?”+ 24 Afarisi atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi. Amatero ndi mphamvu ya Belezebule, wolamulira ziwanda.”+ 25 Podziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha,+ ndipo mzinda uliwonse kapena nyumba yogawanika siikhalitsa. 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagawanika. Nanga tsopano ufumu wake ungakhalepo bwanji? 27 Komanso, ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule,+ nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Pa chifukwa ichi, iwo adzakuweruzani. 28 Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wakufikani modzidzimutsa.+ 29 Kapena munthu angalowe bwanji m’nyumba ya munthu wamphamvu ndi kulanda katundu wake, ngati sangamange munthu wamphamvuyo choyamba? Atam’manga, m’pamene angathe kutenga katundu m’nyumbamo.+ 30 Amene sali kumbali yanga ndi wotsutsana ndi ine, ndipo amene sagwira limodzi ndi ine ntchito yosonkhanitsa anthu kwa ine amawabalalitsa.+
31 “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti, Anthu adzakhululukidwa tchimo la mtundu uliwonse ndi mawu aliwonse onyoza, koma wonyoza mzimu sadzakhululukidwa.+ 32 Mwachitsanzo, aliyense wolankhula mawu onyoza Mwana wa munthu, adzakhululukidwa.+ Koma aliyense wolankhula monyoza mzimu woyera, sadzakhululukidwa, m’nthawi* ino kapena ikubwerayo.+
33 “Anthu inu mumachititsa mtengo ndi zipatso zake kukhala zabwino, kapena mumavunditsa mtengo ndi zipatso zake, chifukwa mtengo umadziwika ndi zipatso zake.+ 34 Ana a njoka inu,+ mungalankhule bwanji zinthu zabwino, pamene muli oipa?+ Pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+ 35 Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chake chabwino,+ koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma chake choipa.+ 36 Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu pa mawu alionse opanda pake amene iwo amalankhula.+ 37 Pakuti ndi mawu ako udzaweruzidwa kuti ndiwe wolungama, ndipo ndi mawu akonso udzaweruzidwa kuti ndiwe wolakwa.”+
38 Tsopano alembi ndi Afarisi ena anamupempha kuti: “Mphunzitsi, tikufuna mutionetse chizindikiro.”+ 39 Poyankha iye anawauza kuti: “M’badwo woipa ndi wachigololo+ ukufunitsitsabe chizindikiro. Sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse koma chizindikiro cha mneneri Yona chokha.+ 40 Pakuti monga momwe Yona+ anakhalira m’mimba mwa chinsomba chachikulu masiku atatu, usana ndi usiku, chimodzimodzinso Mwana wa munthu+ adzakhala mumtima wa dziko lapansi+ masiku atatu, usana ndi usiku.+ 41 Anthu a ku Nineve adzaimirira pa chiweruzo limodzi ndi m’badwo uwu+ ndipo adzautsutsa,+ chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano. 42 Mfumukazi ya kum’mwera+ adzaiukitsa kwa akufa limodzi ndi m’badwo uwu ndipo idzautsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+
43 “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo ouma kufunafuna malo okhala, ndipo supeza alionse.+ 44 Ndiyeno umati, ‘Ndibwerera kunyumba yanga imene ndinatulukamo ija.’ Ukafika umapeza kuti simukukhala aliyense koma ndi mosesedwa bwino ndi mokongoletsedwa. 45 Ukatero umapita kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambiri kuposa umenewo.+ Ikalowa mkatimo imakhala mmenemo ndipo potsirizira pake zochita za munthuyo zimakhala zoipa kwambiri kuposa poyamba.+ Ndi mmenenso zidzakhalira ndi m’badwo woipawu.”+
46 Ali mkati molankhula ndi khamu la anthulo, kunabwera mayi ake ndi abale ake.+ Iwo anaima panja kufuna kuti alankhule naye. 47 Chotero munthu wina anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu aima panjapa, akufuna kulankhula nanu.” 48 Poyankha iye anauza munthu uja kuti: “Kodi mayi anga ndani, ndipo abale anga ndani?”+ 49 Kenako anatambasula dzanja lake ndi kuloza ophunzira ake, n’kunena kuti: “Ona! Mayi anga ndi abale anga!+ 50 Pakuti aliyense wochita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, ndi mayi anga.”
13 Tsiku limenelo, Yesu anachoka kunyumba n’kukakhala pansi m’mphepete mwa nyanja. 2 Khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye, mwakuti iye anakwera m’ngalawa n’kukhala pansi,+ ndipo khamu lonse la anthulo linaimirira m’mphepete mwa nyanjayo. 3 Pa nthawiyo anawauza zinthu zambiri mwa mafanizo kuti: “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+ 4 Pamene anali kufesa, mbewu zina zinagwera m’mbali mwa msewu, ndipo kunabwera mbalame ndi kuzidya.+ 5 Zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira, ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+ 6 Koma dzuwa litakwera zinawauka, ndipo chifukwa chopanda mizu zinafota.+ 7 Komanso mbewu zina zinagwera paminga, ndipo mingazo zinakula ndi kulepheretsa mbewuzo kukula.+ 8 Komabe zina zinagwera panthaka yabwino ndipo zinayamba kubala zipatso.+ Mbewu ina inabala zipatso 100, ina 60, ndipo ina 30.+ 9 Amene ali ndi makutu amve.”+
10 Tsopano ophunzira ake anabwera ndi kum’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulankhula nawo mwa mafanizo?”+ 11 Koma iye anawayankha kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira zinsinsi zopatulika+ za ufumu wakumwamba, koma anthu amenewa sanapatsidwe mwayi umenewo.+ 12 Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka.+ Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 13 N’chifukwa chake ndikulankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti ngakhale akuona, kuona kwawo n’kopanda phindu. Ngakhale akumva, kumva kwawo n’kopanda phindu, ndipo sazindikira tanthauzo lake.+ 14 Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pa iwowa, umene umati, ‘Kumva, mudzamva ndithu, koma osazindikira tanthauzo lake. Kuona, mudzaona ndithu, koma osazindikira.+ 15 Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo ndi kumva ndi makutu awo ndi kuzindikira tanthauzo lake m’mitima yawo n’kutembenuka, kuti ine ndiwachiritse.’+
16 “Koma inu ndinu odala chifukwa maso anu amaona,+ komanso makutu anu amamva. 17 Pakuti ndikukuuzani ndithu, Aneneri ambiri+ komanso anthu olungama analakalaka kuti aone zinthu zimene mukuziona inuzi koma sanazione,+ kutinso amve zimene mukumva inuzi koma sanazimve.+
18 “Tsopano inu, mvetserani fanizo la munthu wofesa mbewu.+ 19 Munthu aliyense akamva mawu a ufumu koma osazindikira tanthauzo lake, woipayo+ amabwera n’kukwatula zomwe zafesedwa mumtima wa munthuyo. Izi ndi zofesedwa m’mbali mwa msewu zija. 20 Koma zofesedwa pamiyala, ndi munthu amene wamva mawu ndi kuwavomereza mwamsanga ndiponso mwachimwemwe.+ 21 Komabe pa iye yekha alibe mizu ndipo amapitirizabe kwa kanthawi. Koma pamene chisautso kapena mazunzo zayamba chifukwa cha mawuwo, iye amapunthwa mwamsanga.+ 22 Zimene zafesedwa paminga, ndi munthu amene amamva mawu, koma nkhawa za moyo wa m’nthawi* ino+ ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zimalepheretsa mawuwo kukula, ndipo iye amakhala wosabala zipatso.+ 23 Mbewu zimene zafesedwa panthaka yabwino, ndi munthu amene wamva mawu ndi kuzindikira tanthauzo lake, amene amabaladi zipatso. Uyu zipatso 100, uyo 60, winayo 30.”+
24 Anawafotokozera fanizo linanso, kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda wake.+ 25 Koma anthu ali m’tulo, kunabwera mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole m’munda wa tiriguwo, n’kuchoka. 26 Tsopano mmerawo utakula ndi kutulutsa ngala, namsongole nayenso anaonekera. 27 Ndiye kunabwera akapolo a mwinimunda uja kudzamuuza kuti, ‘Mbuye, kodi simunafese mbewu zabwino m’munda wanuwu?+ Nanga namsongoleyu wachokeranso kuti?’+ 28 Iye anawauza kuti, ‘Munthu wina wodana nane anachita zimenezi.’+ Akapolowo anati, ‘Tsopano kodi mukufuna kuti tipite kukamuzula?’ 29 Koma iye anawayankha kuti, ‘Ayi, kuopera kuti mwina pozula namsongole mungazule pamodzi ndi tirigu. 30 Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. M’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti, Choyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga m’mitolo kuti akatenthedwe.+ Mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.’”+
31 Anawauzanso fanizo lina,+ kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati kanjere ka mpiru*+ kamene munthu anakatenga ndi kukabzala m’munda wake. 32 Kanjere kameneka ndi kakang’ono kwambiri mwa njere zonse, koma kakamera kamakula kwambiri kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo umakhala mtengo, moti mbalame zam’mlengalenga+ zimabwera kudzapeza malo okhala munthambi zake.”+
33 Anawafotokozeranso fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati zofufumitsa,+ zimene mkazi wina anazitenga ndi kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zazikulu zoyezera, ndipo mtanda wonsewo unafufuma.”
34 Yesu analankhula zonsezi ndi khamu la anthulo m’mafanizo. Ndithudi, sanalankhule nawo chilichonse popanda fanizo,+ 35 kuti zikwaniritsidwe zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri amene anati: “Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mafanizo, ndidzafalitsa zinthu zobisika kuchokera pa chiyambi cha dziko lapansi.”+
36 Kenako atauza khamu la anthulo kuti lizipita, analowa m’nyumba. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye ndi kunena kuti: “Timasulireni fanizo lija la namsongole m’munda.” 37 Poyankha iye ananena kuti: “Wofesa mbewu yabwino uja ndi Mwana wa munthu. 38 Munda ndiwo dziko+ ndipo mbewu zabwino ndi ana a ufumu. Koma namsongole ndi ana a woipayo,+ 39 ndipo mdani amene anafesa namsongole ndi Mdyerekezi.+ Nthawi yokolola+ ikuimira mapeto a nthawi* ino,+ ndipo okololawo ndi angelo. 40 Chotero, monga momwe amasonkhanitsira namsongole ndi kumutentha pamoto, zidzakhalanso choncho pa mapeto a nthawi* ino.+ 41 Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake, ndipo adzachotsa mu ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa+ ndiponso anthu osamvera malamulo. 42 Kenako adzawaponya m’ng’anjo yamoto.+ Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.+ 43 Pa nthawi imeneyo olungama adzawala+ kwambiri ngati dzuwa+ mu ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu amve.+
44 “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza n’kuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa+ zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.+
45 “Komanso ufumu wakumwamba uli ngati wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino. 46 Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali,+ anapita mwamsanga n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo.+
47 “Ndiponso ufumu wakumwamba uli ngati khoka loponyedwa m’nyanja limene limasonkhanitsa nsomba zamitundumitundu.+ 48 Likadzaza amalikokera kumtunda ndipo amakhala pansi n’kumasankha zabwino+ ndi kuziika m’mitanga, koma zosafunika+ amazitaya. 49 Ndi mmenenso zidzakhalire pa mapeto a nthawi* ino: Angelo adzapita n’kukachotsa oipa+ pakati pa olungama+ 50 ndipo adzawaponya m’ng’anjo yamoto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.+
51 “Kodi mukumvetsa tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde.” 52 Kenako anawauza kuti: “Popeza kuti zili choncho, mphunzitsi aliyense wa anthu akaphunzitsidwa za ufumu wakumwamba,+ amakhala ngati munthu, mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chake.”+
53 Tsopano Yesu atatsiriza mafanizo amenewa anachoka kumeneko. 54 Atafika m’dera lakwawo+ anayamba kuwaphunzitsa m’sunagoge wawo,+ moti anthu anadabwa ndipo anali kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru ndi ntchito zamphamvu zoterezi anazitenga kuti? 55 Kodi si mwana wa mmisiri wamatabwa uyu?+ Kodi mayi ake si Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? 56 Alongo ake onse sitili nawo konkuno?+ Nanga iyeyu zinthu zonsezi anazitenga kuti?”+ 57 Choncho anayamba kukhumudwa naye.+ Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo kapena m’nyumba mwake, koma kwina.”+ 58 Ndipo sanachite ntchito zamphamvu zambiri kumeneko chifukwa chakuti anthuwo analibe chikhulupiriro.+
14 Pa nthawiyo Herode,* wolamulira chigawo, anamva za Yesu+ 2 ndipo anauza atumiki ake kuti: “Ameneyu ndi Yohane M’batizi. Anauka kwa akufa, ndipo n’chifukwa chake akuchita ntchito zamphamvu.”+ 3 Pakuti Herode anagwira Yohane, kum’manga ndi kum’tsekera m’ndende chifukwa Herode anakwatira Herodiya, mkazi wa m’bale wake Filipo.+ 4 Anachita zimenezi chifukwa Yohane anali kumuuza kuti: “N’kosaloleka kutenga mkaziyu kuti akhale mkazi wanu.”+ 5 Komabe, ngakhale kuti Herode ankafuna kupha Yohane, anaopa khamu la anthu, chifukwa iwo anali kukhulupirira kuti ndi mneneri.+ 6 Koma tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode+ litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa Herode kwambiri, 7 mwakuti analonjeza molumbira kuti adzapatsa mtsikanayo chilichonse chimene angapemphe.+ 8 Tsopano mtsikanayu, mayi wake atachita kum’pangira, anapempha kuti: “Ndipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.”+ 9 Mfumuyo inamva chisoni, koma poganizira lumbiro lake lija ndi anthu amene anali nawo paphwandolo, analamula kuti mutuwo uperekedwe.+ 10 Choncho anatuma munthu kukadula mutu wa Yohane m’ndende. 11 Kenako anabweretsa mutuwo m’mbale ndi kuupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anapita nawo kwa mayi ake.+ 12 Pambuyo pake, ophunzira ake anabwera kudzatenga mtembo wake ndi kukauika m’manda.+ Kenako anapita kukauza Yesu. 13 Yesu atamva zimenezi, anachoka kumeneko pa ngalawa n’kupita kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha.+ Koma khamu la anthu litamva zimenezo, linam’tsatira wapansi kuchokera m’mizinda yawo.
14 Tsopano Yesu atatsika m’ngalawayo anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvera chisoni,+ ndi kuwachiritsira anthu awo odwala.+ 15 Koma chakumadzulo ophunzira ake anabwera kwa iye ndi kunena kuti: “Kuno n’kopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite m’midzimo kuti akagule chakudya.”+ 16 Koma Yesu anawayankha kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.”+ 17 Iwo anamuuza kuti: “Tilibe chilichonse pano, koma mitanda isanu ya mkate ndi nsomba ziwiri zokha basi.”+ 18 Ndiyeno iye anati: “Bweretsani zimenezo kuno.” 19 Kenako analamula khamu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Pamenepo anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija, n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso.+ Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija n’kupatsa ophunzirawo, ndipo iwonso anagawira khamulo.+ 20 Chotero onse anadya n’kukhuta, ndipo anatolera zotsala zodzaza madengu 12.+ 21 Koma amene anadya anali amuna pafupifupi 5,000 osawerengera akazi ndi ana aang’ono.+ 22 Kenako mwamsanga, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti akwere ngalawa ndi kutsogola kupita kutsidya lina, pamene iye anali kuuza anthuwo kuti azipita kwawo.+
23 Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita, anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.+ Ngakhale kuti kunali kutada, iye anakhalabe kumeneko yekhayekha. 24 Pa nthawiyi n’kuti ngalawa ija itapita kutali pakati pa madzi, ndipo inali kukankhidwa mwamphamvu ndi mafunde+ chifukwa anali kulimbana ndi mphepo yamphamvu. 25 Koma pa ulonda wachinayi* m’bandakucha, iye anafika kwa ophunzirawo akuyenda pamwamba pa madzi.+ 26 Pamene ophunzirawo anamuona akuyenda panyanjapo, anavutika mumtima, n’kumanena kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!”+ Ndipo anafuula mwamantha. 27 Koma nthawi yomweyo Yesu anawauza kuti: “Limbani mtima, ndine.+ Musachite mantha.” 28 Pamenepo Petulo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ndinudi, ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” 29 Iye anamuuza kuti: “Bwera!” Nthawi yomweyo Petulo anatsika m’ngalawamo+ n’kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. 30 Koma ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha, ndipo atayamba kumira anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” 31 Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake ndi kum’gwira dzanja n’kumuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”+ 32 Atakwera m’ngalawa, mphepo yamkuntho ija inaleka. 33 Pamenepo amene anali m’ngalawamo anam’gwadira ndi kunena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”+ 34 Ndipo anawolokera kumtunda ku Genesarete.+
35 Anthu a m’dera limeneli atamuzindikira, anatumiza mithenga m’midzi yonse yapafupi, ndipo anthu anam’bweretsera odwala onse.+ 36 Anthu anali kum’pempha kuti angogwira chabe ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo onse amene anaugwira anachiriratu.
15 Pa nthawiyo Afarisi ndi alembi ochokera ku Yerusalemu anabwera kwa Yesu.+ Iwo anam’funsa kuti: 2 “N’chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya miyambo ya makolo? Mwachitsanzo, sasamba m’manja* akafuna kudya chakudya.”+
3 Koma iye anawayankha kuti: “N’chifukwa chiyani inunso mumaphwanya malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?+ 4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+ 5 Koma inu mumanena kuti, ‘Aliyense wouza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ine ndili nacho, chimene ndikanakuthandizirani, ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,” 6 asalemekeze bambo ake.’+ Chotero mwasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha miyambo yanu.+ 7 Onyenga inu!+ Yesaya+ analosera moyenera za inu muja anati, 8 ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine.+ 9 Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’”+ 10 Atanena izi, anaitana khamu la anthu kuti liyandikire, ndipo anawauza kuti: “Mvetserani ndipo muzindikire tanthauzo lake:+ 11 Chimene chimalowa m’kamwa sichiipitsa munthu, koma chotuluka m’kamwa mwake n’chimene chimaipitsa munthu.”+
12 Kenako ophunzira ake anafika ndi kumufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?”+ 13 Koma iye anayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinabzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa.+ 14 Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.”+ 15 Ndiyeno Petulo anam’pempha kuti: “Timasulireni fanizo lija.”+ 16 Pamenepo Yesu ananena kuti: “Kodi inunso mudakali osazindikira?+ 17 Inunso simudziwa kodi kuti chilichonse cholowa m’kamwa chimadutsa m’matumbo ndipo chimakatayidwa kuchimbudzi? 18 Koma zotuluka m’kamwa zimachokera mumtima, ndipo zimenezo zimaipitsa munthu.+ 19 Mwachitsanzo, maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama, ndi zonyoza Mulungu,+ zimachokera mumtima.+ 20 Izi n’zimene zimaipitsa munthu, koma kudya chakudya osasamba m’manja sikuipitsa munthu.”+
21 Tsopano Yesu anachoka kumeneko ndi kupita m’zigawo za Turo ndi Sidoni.+ 22 Ndiyeno kunabwera mayi wina wa ku Foinike+ kuchokera m’zigawo zimenezo ndi kufuula kuti: “Ndichitireni chifundo+ Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi wagwidwa ndi chiwanda mochititsa mantha.” 23 Koma iye sanamuyankhe chilichonse. Choncho ophunzira ake anabwera ndi kum’pempha kuti: “Muuzeni kuti azipita, chifukwa akupitirizabe kufuula m’mbuyo mwathumu.” 24 Poyankha iye anati: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.”+ 25 Mayi uja atafika pafupi, anam’gwadira ndi kunena kuti: “Ambuye, ndithandizeni!”+ 26 Iye anamuyankha kuti: “Si bwino kutenga chakudya cha ana n’kuponyera tiagalu.” 27 Koma mayiyo anati: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa patebulo la ambuye awo.”+ 28 Pamenepo Yesu anamuyankha kuti: “Mayi iwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu. Zimene ukufuna zichitike kwa iwe.” Ndipo kuchokera mu ola limenelo mwana wake anachira.+
29 Atachoka kumeneko, Yesu anafika pafupi ndi nyanja ya Galileya,+ ndipo anakwera m’phiri+ ndi kukhala pansi m’phirimo. 30 Kenako anthu ochuluka anakhamukira kwa iye. Anabwera ndi anthu olumala, othyoka ziwalo, akhungu, osalankhula, ndi ena ambiri osiyanasiyana, moti anawakhazika pamapazi ake mochita ngati akum’ponyera, ndipo anawachiritsa onsewo.+ 31 Khamu la anthulo linadabwa kuona osalankhula akulankhula, olumala akuyenda ndiponso akhungu akuona, ndipo anatamanda Mulungu wa Isiraeli.+
32 Koma Yesu anaitana ophunzira ake n’kunena kuti:+ “Khamu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine masiku atatu tsopano ndipo alibe chakudya. Sindikufuna kuwauza kuti azipita asanadye, chifukwa angalenguke panjira.” 33 Koma ophunzirawo anamuuza kuti: “Kopanda anthu ngati kuno tiipeza kuti mitanda ya mkate yokwanira khamu lonseli?”+ 34 Kenako Yesu anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7, ndi tinsomba towerengeka.” 35 Chotero atauza anthuwo kuti akhale pansi, 36 anatenga mitanda 7 ya mkate ija ndi nsomba zija. Atayamika, anainyemanyema n’kupatsa ophunzirawo ndipo iwo anagawira khamu la anthulo.+ 37 Anthu onsewo anadya ndi kukhuta, moti zotsala zimene anatolera zinadzaza madengu akuluakulu 7.+ 38 Koma amene anadya anali amuna 4,000, osawerengera akazi ndi ana aang’ono. 39 Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita kwawo, iye anakwera ngalawa n’kufika m’zigawo za Magadani.+
16 Kenako Afarisi+ ndi Asaduki anafika kwa Yesu. Pofuna kumuyesa, anam’pempha kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.+ 2 Koma Yesu anawayankha kuti: “[[Kunja kukamada mumanena kuti, ‘Nyengo ikhala yabwino, chifukwa kumwamba kwachita cheza.’ 3 Koma m’mawa mumanena kuti, ‘Lero kukuoneka kuti kugwa mvula, chifukwa kumwamba kwachita cheza koma kuli mdima wamvula.’ Mumadziwa kumasulira kaonekedwe ka kumwamba, koma simungathe kumasulira zizindikiro za nthawi ino.]]*+ 4 M’badwo woipa ndi wachigololo ukufunitsitsabe chizindikiro, koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse+ kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.”+ Atanena izi, anachoka n’kuwasiya.+
5 Tsopano ophunzira ake anawolokera kutsidya lina koma anaiwala kutenga mikate.+ 6 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Khalani maso ndipo samalani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi Asaduki.”+ 7 Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Sitinatenge mikate pobwera kuno.” 8 Yesu anadziwa zimenezi ndipo ananena kuti: “Inu achikhulupiriro chochepa, mulibe mikate. Ndiye n’chifukwa chiyani mukukambirana zimenezi?+ 9 Kodi mfundo yake simukuimvetsabe? Kapena kodi simukukumbukira anthu 5,000 amene anadya mitanda isanu ya mkate, komanso kuchuluka kwa madengu a zotsalira zimene munatolera?+ 10 Kapena kodi simukukumbukira anthu 4,000 amene anadya mitanda 7 ya mkate, komanso kuchuluka kwa madengu akuluakulu a zotsalira zimene munatolera?+ 11 Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindikunena za mitanda ya mkate? Koma samalani ndi zofufumitsa za Afarisi ndi Asaduki.”+ 12 Pamenepo anazindikira kuti sakunena kuti asamale ndi zofufumitsa mitanda ya mkate, koma kuti asamale ndi zimene Afarisi ndi Asaduki amaphunzitsa.+
13 Tsopano atafika m’zigawo za Kaisareya wa Filipi, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndani?”+ 14 Iwo anayankha kuti: “Ena akumanena kuti Yohane M’batizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akuti Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.” 15 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?”+ 16 Poyankha, Simoni Petulo ananena kuti: “Ndinu Khristu,+ Mwana wa Mulungu wamoyo.”+ 17 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, chifukwa si munthu* amene wakuululira zimenezi, koma Atate wanga amene ali kumwamba wachita zimenezi.+ 18 Chotero inenso ndikukuuza kuti, Iwe ndiwe Petulo,+ ndipo pathanthwe+ ili ndidzamangapo mpingo wanga. Zipata za Manda+ sizidzaugonjetsa.+ 19 Ine ndidzakupatsa makiyi a ufumu wakumwamba. Chilichonse chimene udzamanga padziko lapansi chidzakhala chitamangidwa kumwamba, ndipo chilichonse chimene udzamasula padziko lapansi chidzakhala chitamasulidwa kumwamba.”+ 20 Pamenepo analamula ophunzirawo mwamphamvu kuti asauze aliyense kuti iye ndi Khristu.+
21 Kuyambira pamenepo, Yesu Khristu anayamba kuuza ophunzira ake kuti n’koyenera kuti iye apite ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+ 22 Kenako Petulo anamutengera pambali ndi kuyamba kum’dzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.”+ 23 Koma iye anatembenuka n’kuuza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana!+ Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu,+ koma maganizo a anthu.”
24 Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo* ndipo anditsatire mosalekeza.+ 25 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.+ 26 Kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?+ Kapena munthu angapereke chiyani chosinthanitsa+ ndi moyo wake? 27 Pakuti Mwana wa munthu adzabwera ndithu mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo ake. Pa nthawi imeneyo adzapatsa aliyense mphoto malinga ndi makhalidwe ake.+ 28 Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga mfumu.”+
17 Patapita masiku 6 Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane m’bale wake, n’kukwera nawo m’phiri lalitali kwaokhaokha.+ 2 Kumeneko iye anasandulika pamaso pawo, ndipo nkhope yake inawala ngati dzuwa.+ Malaya ake akunja anawala kwambiri.+ 3 Kenako Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akukambirana ndi Yesu.+ 4 Ataona izi, Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndi bwino ife tizikhala pano. Ngati mukufuna, ndimanga mahema atatu pano, limodzi lanu, limodzi la Mose ndi lina la Eliya.”+ 5 Mawu ake adakali m’kamwa, mtambo wowala kwambiri unawaphimba, ndipo panamveka mawu kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye,+ muzimumvera.”+ 6 Ophunzirawo atamva zimenezi, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi ndipo anachita mantha kwambiri.+ 7 Kenako Yesu anawayandikira ndipo anawagwira n’kunena kuti: “Dzukani, musaope.”+ 8 Atakweza maso awo, anaona kuti palibe wina aliyense koma Yesu yekha.+ 9 Pamene anali kutsika m’phirimo, Yesu anawalamula kuti: “Musauze wina aliyense za masomphenya amenewa kufikira Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa.”+
10 Koma ophunzirawo anamufunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya ayenera kubwera choyamba?”+ 11 Poyankha iye anati: “Inde, Eliya adzabweradi ndipo adzabwezeretsa zinthu zonse.+ 12 Komabe, ine ndikukuuzani kuti Eliya anabwera kale ndipo iwo sanamuzindikire koma anam’chitira zilizonse zimene iwo anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa munthu.”+ 13 Pamenepo ophunzirawo anazindikira kuti anali kunena za Yohane M’batizi.+
14 Tsopano atafika kufupi ndi khamu la anthu,+ mwamuna wina anamuyandikira, ndipo anam’gwadira ndi kunena kuti: 15 “Ambuye, muchitire chifundo mwana wanga wamwamuna, chifukwa ndi wakhunyu ndipo akuvutika kwambiri. Amagwera pamoto kawirikawiri ndiponso amagwera m’madzi kawirikawiri.+ 16 Ndinabwera naye kwa ophunzira anu, koma alephera kumuchiritsa.”+ 17 Poyankha Yesu anati: “Inu a m’badwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.” 18 Pamenepo Yesu anadzudzula chiwandacho, ndipo chinatuluka.+ Nthawi yomweyo mnyamatayo anachira.+ 19 Pambuyo pake ophunzira anabwera kwa Yesu paseri ndi kunena kuti: “N’chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?”+ 20 Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Pakuti ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.”+ 21* ——
22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu,+ 23 ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Atamva zimenezi iwo anamva chisoni kwambiri.+
24 Atafika ku Kaperenao, anthu okhometsa msonkho wa madalakima awiri anafikira Petulo ndi kumufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu amapereka madalakima awiri a msonkho?”+ 25 Iye anati: “Inde amapereka.” Koma atalowa m’nyumba, asananene chilichonse, Yesu anamufunsa kuti: “Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko lapansi amalandira ndalama za ziphaso kapena za msonkho kuchokera kwa ndani? Kuchokera kwa ana awo kapena kwa anthu achilendo?” 26 Atayankha kuti: “Kuchokera kwa anthu achilendo,” Yesu anamuuza kuti: “Choterotu ana sayenera kukhoma msonkho. 27 Koma kuti tisawakhumudwitse,+ pita kunyanja, ukaponye mbedza, ndipo ukatenge nsomba yoyambirira kuwedza. Ukakaikanula kukamwa kwake, ukapezako khobidi limodzi lasiliva.* Ukalitenge n’kukhomera msonkho wako ndi wanga.”+
18 Pa nthawi imeneyo, ophunzira anayandikira Yesu ndi kunena kuti: “Ndani kwenikweni amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba?”+ 2 Pamenepo iye anaitana mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo+ 3 ndi kunena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Mukapanda kutembenuka n’kukhala ngati ana aang’ono,+ simudzalowa mu ufumu wakumwamba.+ 4 Chotero, aliyense amene adzadzichepetsa+ ngati mwana wamng’ono uyu ndi amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba.+ 5 Ndiponso aliyense wolandira mwana wamng’ono ngati ameneyu m’dzina langa walandiranso ine.+ 6 Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana iti timene timakhulupirira mwa ine, zingamukhalire bwino kwambiri kumumangirira chimwala cha mphero+ m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kumumiza m’nyanja yaikulu.+
7 “Tsoka dzikoli chifukwa cha zopunthwitsa! Inde sitingachitire mwina, zopunthwitsazo ziyenera kubwera ndithu,+ koma tsoka lili kwa munthu wobweretsa chopunthwitsa!+ 8 Chotero ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule ndi kulitaya kutali.+ Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi kapena uli wolumala kusiyana ndi kuti ukaponyedwe m’moto wosatha uli ndi manja onse awiri kapena mapazi onse awiri.+ 9 Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa ulikolowole n’kulitaya. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli ndi diso limodzi kusiyana ndi kuti ukaponyedwe mu Gehena* wamoto uli ndi maso onse awiri.+ 10 Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo+ kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.+ 11* ——
12 “Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera,+ kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo?+ 13 Akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zosasochera zija.+ 14 Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.+
15 “Komanso, ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo.+ Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo.+ 16 Koma akapanda kukumvera, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.+ 17 Akapanda kuwamvera amenewanso, uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvera mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina+ komanso ngati wokhometsa msonkho.+
18 “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, zilizonse zimene mudzamanga padziko lapansi zidzakhala zitamangidwa kumwamba, ndipo zilizonse zimene mudzamasula padziko lapansi zidzakhala zitamasulidwa kumwamba.+ 19 Ndiponso ndikukuuzani kuti, ngati awiri mwa inu padziko lapansi pano adzagwirizana pa chilichonse chofunika kupempha, Atate wanga wakumwamba adzawachitira.+ 20 Pakuti kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa,+ ine ndidzakhala pakati pawo.”+
21 Kenako Petulo anabwera kwa iye ndi kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga angandichimwire kangati ndipo ine n’kumukhululukira?+ Mpaka nthawi 7 kodi?”+ 22 Yesu anayankha kuti: “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, Mpaka nthawi 77.+
23 “N’chifukwa chake ufumu wakumwamba uli ngati mfumu+ imene inafuna kuti akapolo ake abweze ngongole.+ 24 Itayamba kulandira ngongolezo, atumiki ake anabweretsa munthu amene anali ndi ngongole ya matalente 10,000 [omwe ndi madinari 60 miliyoni] kwa mfumuyo. 25 Koma popeza kuti analibe choti apereke pobweza ngongoleyo, mbuye wake analamula kuti mwamuna ameneyu, mkazi wake, ana ake komanso zonse zimene anali nazo zigulitsidwe ndi kum’bwezera ndalama zake.+ 26 Pamenepo kapoloyu anagwada pansi ndi kuyamba kumuweramira n’kunena kuti, ‘Ndilezereniko mtima chonde, ndidzakubwezerani zonse.’ 27 Izi zinamvetsa chisoni mbuyeyo ndipo anamusiya kapoloyo+ ndi kumukhululukira ngongole yake ija.+ 28 Koma kapoloyo atatuluka anakumana ndi kapolo mnzake amene iye anamukongoza madinari 100.+ Iye anamugwira ndi kumukanyanga pakhosi, n’kunena kuti, ‘Bweza ngongole ija mwamsanga.’ 29 Kapolo mnzakeyo anagwada pansi ndi kuyamba kumudandaulira kuti, ‘Mundilezereko mtima chonde,+ ndidzakubwezerani.’ 30 Koma iye sanalole, ndipo anapita kukam’pereka kundende mpaka pamene adzabweze ngongoleyo. 31 Akapolo anzake ataona zimene zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita kwa mbuye wawo ndi kukafotokoza zonse zimene zinachitika.+ 32 Ndiyeno mbuye wakeyo anamuitanitsa ndi kumuuza kuti, ‘Kapolo woipa iwe, ine ndakukhululukira ngongole yonse ija utandidandaulira. 33 Kodi nawenso sukanam’chitira chifundo+ kapolo mnzako, monga momwe ine ndinakuchitira chifundo?’+ 34 Pamenepo mbuye wakeyo anakwiya,+ ndipo anamupereka kwa oyang’anira ndende, mpaka pamene adzabweze ngongole yonse. 35 Mofanana ndi zimenezi,+ Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.”+
19 Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, anachoka ku Galileya ndi kubwera kumadera a kumalire kwa Yudeya kutsidya la Yorodano.+ 2 Khamu lalikulu la anthu linam’tsatira, ndipo iye anawachiritsa kumeneko.+
3 Afarisi anabwera kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”+ 4 Yesu anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi+ 5 n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake+ n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’?+ 6 Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”+ 7 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipereka kalata yothetsa ukwati kwa mkazi ndi kum’siya?”+ 8 Iye anayankha kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu,+ Mose anakulolezani kuti muzithetsa ukwati, koma kuyambira pa chiyambi sizinali choncho ayi.+ 9 Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”*+
10 Kenako ophunzira ake anati: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino kusakwatira.”+ 11 Iye anawauza kuti: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.+ 12 Pakuti ena sakwatira chifukwa chakuti anabadwa choncho kuchokera m’mimba mwa mayi awo,+ ndipo ena chifukwa chakuti anafulidwa ndi anthu. Koma pali ena amene safuna kukwatira chifukwa cha ufumu wakumwamba. Amene angathe kuchita zimenezi achite.”+
13 Kenako anthu anam’bweretsera ana aang’ono kuti awaike manja ndi kuwapempherera, koma ophunzirawo anawakalipira.+ 14 Koma Yesu anawauza kuti: “Alekeni anawo, ndipo musawaletse kubwera kwa ine, pakuti ufumu wakumwamba ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.”+ 15 Pamenepo anaika manja ake pa anawo, kenako anachoka kumeneko.+
16 Tsopano munthu wina anafika kwa iye ndi kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, n’chiyani chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 17 Iye anamuyankha kuti: “N’chifukwa chiyani ukundifunsa chimene chili chabwino? Pali Mmodzi yekha amene ali wabwino.+ Chotero ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.”+ 18 Koma iye anafunsa Yesu kuti: “Malamulo ati?”+ Yesu anati: “Akuti, Usaphe+ munthu,* Usachite chigololo,+ Usabe,+ Usapereke umboni wonamizira mnzako.+ 19 Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,+ komanso lakuti, Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 20 Mnyamatayo anayankha Yesu kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, n’chiyaninso chimene ndikupereweza?” 21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22 Mnyamata uja atamva mawu amenewa, anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+ 23 Koma Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani, zidzakhalatu zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu ufumu wakumwamba.+ 24 Ndiponso ndikukuuzani kuti, N’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”+
25 Ophunzirawo atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anati: “Ndiye angapulumuke ndani?”+ 26 Yesu anawayang’anitsitsa n’kunena kuti: “Kwa anthu zimenezi n’zosathekadi, koma zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”+
27 Pamenepo Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani, kodi tidzapeza chiyani?”+ 28 Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wachifumu waulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.+ 29 Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kwambiri kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.+
30 “Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza, ndipo omaliza adzakhala oyamba.+
20 “Pakuti ufumu wakumwamba uli ngati mwinimunda wa mpesa, amene analawirira m’mawa kwambiri kukafuna anthu aganyu kuti akagwire ntchito m’munda wake wa mpesa.+ 2 Aganyu amenewa atagwirizana nawo kuti aziwapatsa ndalama ya dinari imodzi pa tsiku,+ anawatumiza kumunda wake wa mpesa. 3 Pafupifupi 9 koloko m’mawa*+ anapitanso kukafuna anthu ena, ndipo anaona ena atangoimaima pamsika alibe chochita.+ 4 Amenewonso anawauza kuti, ‘Inunso kagwireni ntchito m’munda wa mpesa. Ndidzakupatsani malipiro oyenerera.’ 5 Chotero iwo anapita. Pafupifupi 12 koloko+ ndi 3 koloko masana,*+ mwinimunda uja anapitanso kukachita chimodzimodzi. 6 Pamapeto pake, pafupifupi 5 koloko madzulo* anapitanso ndipo anakapeza ena atangoimaima. Iye anawafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwangoimaima pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ 7 Iwo anamuyankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba ganyu.’ Iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani kumunda wanga wa mpesa.’+
8 “Madzulowo,+ mwinimunda wa mpesa uja anauza kapitawo wake kuti, ‘Itana antchito aja uwapatse malipiro awo,+ kuyambira omalizira, kutsiriza ndi oyambirira.’ 9 Anthu amene anayamba ntchito 5 koloko aja atafika, aliyense analandira dinari imodzi. 10 Chotero oyambirira aja atafika, anaganiza kuti alandira zambiri, koma nawonso malipiro amene analandira anali dinari imodzi. 11 Atalandira, anayamba kung’ung’udza kwa mwinimunda wa mpesa uja+ 12 kuti, ‘Omalizirawa agwira ntchito ola limodzi lokha, koma mwawapatsa malipiro ofanana ndi ife amene tagwira ntchito yakalavulagaga tsiku lonse padzuwa lotentha!’ 13 Koma poyankha kwa mmodzi wa iwo, mwinimundayo anati, ‘Bwanawe, sindikukulakwira ayi. Tinapangana malipiro a dinari imodzi, si choncho kodi?+ 14 Ingolandira malipiro ako uzipita. Ndikufuna kupatsa womalizirayu malipiro ofanana ndi amene ndapereka kwa iwe.+ 15 Kodi n’kosaloleka kuchita zimene ndikufuna ndi zinthu zanga? Kapena diso lako lachita njiru+ chifukwa chakuti ndine wabwino?’+ 16 Choncho omalizira adzakhala oyambirira ndipo oyambirira adzakhala omalizira.”+
17 Ali panjira yopita ku Yerusalemu, Yesu anatengera pambali ophunzira ake 12+ aja n’kuwauza kuti: 18 “Tsopano tikupita ku Yerusalemu. Kumeneku, Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo akamuweruza kuti aphedwe.+ 19 Akam’pereka kwa anthu a mitundu ina kuti am’chitire chipongwe, kum’kwapula ndi kum’pachika pamtengo,+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+
20 Kenako mkazi wa Zebedayo+ anafika kwa Yesu ndi ana ake aamuna, ndipo anamugwadira ndi kum’pempha kanthu kena.+ 21 Iye anafunsa mayiyo kuti: “Mukufuna chiyani?” Mayiyo anati: “Lonjezani kuti ana angawa adzakhala, mmodzi kudzanja lanu lamanja, wina kumanzere kwanu, mu ufumu wanu.”+ 22 Koma Yesu anayankha kuti: “Anthu inu simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwe+ zimene ine ndatsala pang’ono kumwa?” Iwo anati: “Inde tingamwe.” 23 Iye anawauza kuti: “Inde mudzamwadi+ zimene ndatsala pang’ono kumwa. Koma kunena zokhala kudzanja langa lamanja ndi lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo, koma Atate wanga adzaupereka kwa amene anawakonzera.”+
24 Ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya ndi amuna awiri apachibalewo.+ 25 Koma Yesu anawaitana n’kuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 26 Sizili choncho pakati panu,+ koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu.+ 27 Amene akufuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wanu.+ 28 Mofanana ndi zimenezi, Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira+ ndi kudzapereka moyo wake dipo* kuwombola anthu ambiri.”+
29 Tsopano pamene iwo anali kutuluka mu Yeriko,+ khamu lalikulu la anthu linam’tsatira. 30 Ndiyeno amuna awiri akhungu anakhala pansi m’mphepete mwa msewu ndipo atamva kuti Yesu akudutsa, anafuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”+ 31 Pamenepo khamu la anthulo linawakalipira kuti akhale chete, koma m’pamene anafuula kwambiri kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”+ 32 Choncho Yesu anaima, ndipo anawaitana ndi kuwafunsa kuti: “Mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” 33 Iwo anamuyankha kuti: “Ambuye, titseguleni maso athu.”+ 34 Atagwidwa ndi chifundo, Yesu anagwira maso awo.+ Nthawi yomweyo akhunguwo anayamba kuona ndipo anam’tsatira.+
21 Tsopano anayandikira ku Yerusalemu, ndipo atafika ku Betefage paphiri la Maolivi, Yesu anatuma ophunzira awiri+ 2 n’kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi umene mukuuonawo. Kumeneko mukapeza bulu atam’mangirira limodzi ndi mwana wake wamphongo. Mukawamasule ndi kuwabweretsa kwa ine.+ 3 Wina aliyense akakakufunsani chilichonse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza kuno.”
4 Izi zinachitikadi kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri zikwaniritsidwe, zakuti: 5 “Uzani mwana wamkazi wa Ziyoni kuti, ‘Taona! Mfumu yako ikubwera kwa iwe.+ Ndi yofatsa+ ndipo yakwera bulu wamng’ono wamphongo, mwana wa nyama yonyamula katundu.’”+
6 Choncho ophunzirawo ananyamuka ndi kukachita zimene Yesu anawalamula. 7 Iwo anabweretsa bulu uja limodzi ndi mwana wake wamphongo. Kenako anayala malaya awo akunja pa abuluwo ndipo iye anakwerapo.+ 8 Anthu ambiri m’khamulo anayala malaya awo akunja+ mumsewu ndipo ena anayamba kudula nthambi za mitengo n’kuziyala mumsewu.+ 9 Koma khamu la anthu, limene linali patsogolo pake ndi m’mbuyo mwake linali kufuula kuti: “M’pulumutseni+ Mwana wa Davide!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!*+ M’pulumutseni kumwambamwambako!”+
10 Tsopano atalowa mu Yerusalemu,+ mzinda wonse unagwedezeka. Ena anali kufunsa kuti: “Kodi ameneyu ndani?” 11 Khamu la anthulo linali kuyankha kuti: “Ameneyu ndi mneneri+ Yesu, wochokera ku Nazareti, ku Galileya!”
12 Kenako Yesu analowa m’kachisi ndi kuthamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda.+ 13 Iye anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”+ 14 Anthu akhungu ndi olumala anabwera kwa iye m’kachisimo, ndipo anawachiritsa.
15 Ansembe aakulu ndi alembi ataona zodabwitsa zimene anachitazo+ komanso anyamata amene anali kufuula m’kachisimo kuti: “M’pulumutseni+ Mwana wa Davide!”+ anakwiya kwambiri 16 ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukumva zimene awa akunenazi?” Yesu anayankha kuti: “Inde. Kodi simunawerenge+ zimenezi kuti, ‘M’kamwa mwa ana ndi mwa ana oyamwa mwaikamo mawu otamanda’?”+ 17 Kenako iye anawasiya n’kutuluka mumzindawo kupita ku Betaniya, ndipo anagona kumeneko.+
18 Pamene anali kubwerera kumzinda uja m’mawa, anamva njala.+ 19 Kenako anaona mkuyu m’mbali mwa msewu ndipo atapita pomwepo, sanapezemo chilichonse+ koma masamba okhaokha. Choncho anauza mtengowo kuti: “Kuyambira lero sudzabalanso zipatso kwamuyaya.”+ Ndipo mkuyuwo unafota nthawi yomweyo. 20 Ophunzira aja ataona zimenezi, anadabwa ndi kunena kuti: “Zatheka bwanji kuti mkuyuwu ufote nthawi yomweyi?”+ 21 Poyankha Yesu ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro, osakayika,+ mudzatha kuchita zimene ndachitira mkuyu umenewu. Komanso kuposa pamenepa, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzachitikadi.+ 22 Chinthu chilichonse chimene mudzapempha m’mapemphero anu, mudzalandira ngati muli ndi chikhulupiriro.”+
23 Tsopano Yesu analowa m’kachisi, ndipo pamene anali kuphunzitsa, ansembe aakulu ndiponso akulu anabwera kwa iye ndi kumufunsa kuti:+ “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 24 Poyankha Yesu anati: “Inenso ndikufunsani chinthu chimodzi. Mukandiuza chinthu chimenecho, inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi:+ 25 Kodi ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”+ Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+ 26 Komanso sitinganene kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ chifukwa tikuopa khamu la anthuli,+ pakuti onsewa amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”+ 27 Chotero poyankha Yesu, iwo anati: “Sitikudziwa.” Nayenso anati: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.+
28 “Kodi mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana awiri.+ Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti: ‘Mwana wanga, lero upite kukagwira ntchito m’munda wa mpesa.’ 29 Iye poyankha anati, ‘Ndipita bambo,’+ koma sanapite. 30 Kenako anapita kwa mwana wachiwiri uja n’kumuuzanso chimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Ayi sindipita.’ Koma pambuyo pake anamva chisoni+ ndipo anapita. 31 Ndani mwa ana awiriwa amene anachita chifuniro cha bambo ake?”+ Iwo anati: “Wachiwiriyu.” Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndi mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukalowa mu ufumu wa Mulungu. 32 Pakuti Yohane anabwera kwa inu m’njira yachilungamo,+ koma inu simunam’khulupirire.+ Koma okhometsa msonkho ndi mahule anam’khulupirira,+ Ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve chisoni n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupirire.
33 “Mverani fanizo lina: Panali munthu wina yemwe analima munda wa mpesa+ ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa ndi kumanga nsanja.+ Atatero anausiya m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina.+ 34 Nyengo ya zipatso itafika, anatumiza akapolo ake kwa alimiwo kuti akatenge zipatso zake. 35 Koma alimi aja anagwira akapolo ake aja ndipo mmodzi anam’menya, wina anamupha, wina anam’ponya miyala.+ 36 Anatumizanso akapolo ena ambiri kuposa oyamba aja, koma amenewa anawachitanso chimodzimodzi.+ 37 Pamapeto pake anawatumizira mwana wake, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 38 Alimiwo ataona mwanayo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe ndi kutenga cholowa chakecho!’+ 39 Choncho anamugwira ndi kum’tulutsa m’munda wa mpesawo n’kumupha.+ 40 Chotero, kodi mwinimunda wa mpesa uja akadzabwera, adzachita nawo chiyani alimiwo?” 41 Iwo anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndi oipa, adzawawononga koopsa+ ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa alimi ena, amene angam’patse zipatso m’nyengo yake.”+
42 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunawerenge zimene Malemba amanena zakuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana+ ndi umene wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.+ Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’? 43 Ichi n’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.+ 44 Komanso munthu wogwera pamwala umenewu adzaphwanyika. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, udzamupereratu.”+
45 Tsopano ansembe aakulu ndi Afarisi atamvetsera mafanizo akewa, anazindikira kuti anali kunena za iwo.+ 46 Komabe, ngakhale kuti anali kufunafuna mpata wakuti amugwire, ankaopa khamu la anthu, chifukwa anthuwo anali kukhulupirira kuti iye ndi mneneri.+
22 Popitiriza kuwayankha, Yesu anawauzanso mafanizo ena kuti:+ 2 “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati+ wa mwana wake. 3 Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando laukwati,+ koma anthuwo sanafune kubwera.+ 4 Kenako inatumanso akapolo ena+ kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana,+ ng’ombe zanga komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani ku phwando laukwati.”’+ 5 Koma anthuwo ananyalanyaza ndi kuchoka. Wina anapita kumunda wake, wina kumalonda ake.+ 6 Koma enawo anagwira akapolo akewo, ndi kuwachitira zachipongwe n’kuwapha.+
7 “Pamenepo mfumu ija inakwiya kwambiri, ndipo inatumiza asilikali ake kukawononga opha anthu amenewo ndi kutentha mzinda wawo.+ 8 Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa ndithu, koma oitanidwa aja anali osayenera.+ 9 Chotero pitani m’misewu yotuluka mumzinda, ndipo aliyense amene mukam’peze, mukamuitanire phwando laukwatili.’+ 10 Choncho akapolowo anapita m’misewu ndi kusonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe.+ Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu oyembekezera kulandira chakudya.+
11 “Pamene mfumu ija inalowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati.+ 12 Chotero inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’+ Iye anasowa chonena. 13 Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja ndi miyendo ndipo mum’ponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’+
14 “Pakuti oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.”+
15 Pamenepo Afarisi anachoka ndi kukapangana kuti am’kole m’mawu ake.+ 16 Choncho anamutumizira ophunzira awo, limodzi ndi achipani cha Herode,+ ndipo iwo anati: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu m’choonadi, ndiponso simusamala kuti uyu ndani, chifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu.+ 17 Ndiye tatiuzani, Mukuganiza bwanji? Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”+ 18 Koma Yesu, podziwa kuipa mtima kwawo, ananena kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa?+ 19 Ndionetseni khobidi la msonkho.” Pamenepo anam’bweretsera khobidi limodzi la dinari. 20 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi ndi mawu akewa n’zandani?”+ 21 Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Pamenepo iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”+ 22 Atamva zimenezi, anadabwa ndipo anangochokapo n’kumusiya.+
23 Pa tsikulo Asaduki, amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa iye n’kumufunsa kuti:+ 24 “Mphunzitsi, Mose anati, ‘Ngati munthu wamwalira wopanda ana, m’bale wake ayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana.’+ 25 Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako n’kumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkazi uja anakwatiwa ndi m’bale wa mwamuna wake.+ 26 Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja.+ 27 Pamapeto pake mkaziyo nayenso anamwalira. 28 Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”+
29 Koma Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.+ 30 Pakuti pouka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa,+ koma adzakhala ngati angelo akumwamba. 31 Kunena za kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,+ 32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?+ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.”+ 33 Pakumva zimenezo, khamu la anthulo linadabwa ndi zimene anali kuphunzitsa.+
34 Afarisi atamva kuti Yesu anawasowetsa chonena Asaduki, anasonkhana monga gulu limodzi. 35 Ndipo mmodzi wa iwo, wodziwa Chilamulo,+ anafunsa Yesu momuyesa kuti: 36 “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?”+ 37 Iye anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova* Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’+ 38 Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. 39 Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ 40 Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso Zolemba za aneneri.”+
41 Tsopano Afarisi aja atasonkhana pamodzi Yesu anawafunsa kuti:+ 42 “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi mwana wa Davide.”+ 43 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu,+ Davide anamutcha ‘Ambuye,’ muja anati, 44 ‘Yehova wauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’?+ 45 Chotero ngati Davide anamutcha kuti ‘Ambuye,’ akukhala bwanji mwana wake?”+ 46 Koma panalibe ngakhale mmodzi amene anatha kumuyankha, ndipo kuchokera tsiku limenelo palibe amene analimbanso mtima kumufunsa mafunso.+
23 Pambuyo pake Yesu analankhula kwa khamu la anthu ndi kwa ophunzira ake+ kuti: 2 “Alembi+ ndi Afarisi adzikhazika pampando wa Mose.+ 3 Chotero muzichita ndi kutsatira zilizonse zimene angakuuzeni,+ koma musamachite zimene iwo amachita,+ chifukwa iwo amangonena koma osachita. 4 Iwo amamanga akatundu olemera ndi kusenzetsa anthu pamapewa,+ koma eni akewo safuna kusuntha akatunduwo ndi chala chawo.+ 5 Zonse zimene amachita, amazichita kuti anthu awaone.+ Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba+ timene amavala monga zodzitetezera, ndipo amakulitsanso ulusi wopota wa m’mphepete+ mwa zovala zawo. 6 Amakonda malo olemekezeka kwambiri+ pa chakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge.+ 7 Amakondanso kupatsidwa moni+ m’misika komanso kuti anthu aziwatchula kuti Rabi.+ 8 Koma inu musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha,+ ndipo nonsenu ndinu abale. 9 Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi,+ wakumwamba Yekhayo. 10 Musamatchedwe ‘atsogoleri,’+ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu. 11 Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu.+ 12 Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa,+ koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.+
13 “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mukutseka+ ufumu wakumwamba kuti anthu asalowemo. Pakuti inuyo+ simukulowamo, mukuletsa amene akufuna kulowamo kuti asalowe. 14* ——
15 “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumatha mitunda kuti mukatembenuze munthu mmodzi, koma akatembenuka mumam’sandutsa woyenera kuponyedwa m’Gehena* kuposa inuyo.
16 “Tsoka kwa inu atsogoleri akhungu,+ amene mumati, ‘Ngati munthu walumbirira kachisi palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira golide wa m’kachisi, asunge lumbiro lake.’+ 17 Opusa ndi akhungu inu! Chofunika kwambiri n’chiti, golide kapena kachisi amene wayeretsa golideyo?+ 18 Komanso mumati, ‘Ngati munthu walumbirira guwa lansembe, palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira mphatso imene ili paguwapo, asunge lumbiro lake.’ 19 Akhungu inu! Chofunika kwambiri n’chiti, mphatso kapena guwa lansembe+ limene limayeretsa mphatsoyo? 20 Chotero amene walumbirira guwa lansembe walumbirira guwalo ndi zonse zimene zili pamenepo, 21 ndipo amene walumbirira kachisi walumbirira kachisiyo limodzi ndi iye amene amakhala mmenemo.+ 22 Wolumbirira kumwamba walumbirira mpando wachifumu wa Mulungu+ komanso amene akukhala pampandowo.
23 “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumapereka chakhumi+ cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika.+ Kupereka zinthu zimenezi n’kofunikadi, koma osanyalanyaza zinthu zinazo. 24 Atsogoleri akhungu inu,+ amene mumasefa zakumwa zanu kuti muchotsemo kanyerere+ koma mumameza ngamila.+
25 “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumayeretsa kunja kwa kapu+ ndi mbale, koma mkati mwake mutadzaza zolanda+ ndi kusadziletsa. 26 Mfarisi wakhungu+ iwe, yeretsa mkati mwa kapu+ ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera.
27 “Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumafanana ndi manda opaka laimu,+ amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zamitundu yonse. 28 Mofanana ndi zimenezi inunso, pamaso pa anthu, mumaonekadi ngati olungama+ koma mkati mwanu mwadzaza chinyengo ndi kusamvera malamulo.
29 “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumamanga manda a aneneri ndi kukongoletsa manda achikumbutso a anthu olungama,+ 30 ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako m’masiku a makolo athu, ifeyo sitikanakhudzidwa ndi mlandu wawo wokhetsa magazi a aneneri.’+ 31 Chotero mukudzichitira nokha umboni kuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneri.+ 32 Choncho malizitsani ntchito+ imene makolo anu anayamba.
33 “Njoka inu, ana a mphiri,+ mudzathawa bwanji chiweruzo cha Gehena?+ 34 Pa chifukwa chimenechi, tsopano ndikukutumizirani+ aneneri, anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ ndi kuwapachika, ndipo ena mudzawakwapula+ m’masunagoge mwanu ndi kuwazunza mumzinda ndi mzinda, 35 kuti magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu,+ kuyambira magazi a Abele+ wolungama+ mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene inu munamupha pakati pa nyumba yopatulika ndi guwa lansembe.+ 36 Ndithu ndikukuuzani kuti, Zinthu zonsezi zidzaubwerera m’badwo uwu.+
37 “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe+ ndi woponya miyala+ anthu otumizidwa kwa iwe.+ Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko.+ Koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 38 Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani+ nyumba* yanuyi.+ 39 Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano simudzandionanso kufikira pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!’”+
24 Tsopano Yesu anayamba ulendo kuchoka kukachisiko. Kenako ophunzira ake anabwera pafupi naye kuti amuonetse nyumba za pakachisipo.+ 2 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simukuziona zinthu zonsezi? Ndithu ndikukuuzani, Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+
3 Atakhala pansi m’phiri la Maolivi, ophunzira anafika kwa iye mwamseri ndi kunena kuti: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo* kwanu+ ndi cha mapeto a nthawi* ino chidzakhala chiyani?”+
4 Poyankha Yesu ananena kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni,+ 5 chifukwa ambiri adzabwera m’dzina langa ndi kunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+ 6 Mudzamva phokoso la nkhondo ndi mbiri za nkhondo. Izitu zisadzakuchititseni mantha. Pakuti zimenezi ziyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+
7 “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina,+ ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ Kudzakhala njala+ ndi zivomezi+ m’malo osiyanasiyana. 8 Zonsezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.
9 “Kenako anthu adzakuperekani ku chisautso+ ndipo adzakuphani.+ Mitundu yonse idzadana nanu+ chifukwa cha dzina langa.+ 10 Komanso, pa nthawiyo anthu ambiri adzapunthwa+ ndipo adzaperekana ndi kudana.+ 11 Kudzafika aneneri ambiri onyenga+ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+ 12 Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo,+ chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.+ 13 Koma amene adzapirire+ mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.+ 14 Uthenga wabwino+ uwu wa ufumu+ udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse,+ kenako mapeto+ adzafika.
15 “Choncho, mukadzaona chinthu chonyansa+ chowononga chimene chinanenedwa kudzera mwa mneneri Danieli chitaimirira m’malo oyera,+ (wowerenga adzazindikire,) 16 amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira+ kumapiri. 17 Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kukatenga katundu m’nyumba mwake. 18 Munthu amene ali m’munda asadzabwerere kunyumba kukatenga malaya ake akunja. 19 Tsoka kwa akazi apakati ndi oyamwitsa ana m’masiku amenewo!+ 20 Pitirizani kupemphera kuti musadzathawe m’nyengo ya chisanu kapena pa tsiku la sabata. 21 Pakuti pa nthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu+ chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano,+ ndipo sichidzachitikanso. 22 Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo,+ masikuwo adzafupikitsidwa.+
23 “Chotero munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’+ kapena, ‘Ali uko!’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 24 Pakuti kudzafika onamizira kukhala Khristu+ ndi aneneri onyenga,+ ndipo adzachita zizindikiro zamphamvu+ ndiponso zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.+ 25 Onani! Ine ndakuchenjezeranitu.+ 26 Chotero anthu akadzakuuzani kuti, ‘Taonani! Ali m’chipululu,’ musadzapiteko. Akadzati, ‘Taonani! Ali m’zipinda zamkati,’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 27 Pakuti mmene mphezi+ imang’animira kuchokera kum’mawa, ndi kuwala mpaka kumadzulo, zidzakhalanso choncho ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.+ 28 Kulikonseko kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga+ zimasonkhana komweko.+
29 “Chisautso cha masiku amenewo chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima+ ndipo mwezi+ sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka.+ 30 Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa munthu+ chidzaonekera kumwamba. Ndiyeno mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni,+ ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.+ 31 Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga,+ ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake+ kuchokera kumphepo zinayi,+ kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.
32 “Tsopano phunzirani mfundo imeneyi pa fanizo ili la mkuyu: Nthambi yake yanthete ikaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi.+ 33 Inunso chimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.+ 34 Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu+ sudzatha wonse kuchoka kufikira zinthu zonsezi zitachitika. 35 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka,+ koma mawu anga sadzachoka ayi.+
36 “Kunena za tsikulo ndi ola lake,+ palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.+ 37 Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa,+ ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.+ 38 M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa+ analowa m’chingalawa.+ 39 Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.+ Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu. 40 Pa nthawiyo, amuna awiri adzakhala ali m’munda, wina adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa. 41 Akazi awiri adzakhala akupera pamphero+ wina adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa.+ 42 Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.+
43 “Koma dziwani ichi: Ngati mwininyumba angadziwe nthawi yobwera mbala,+ angakhale maso ndipo sangalole kuti mbala zithyole ndi kulowa m’nyumba mwake. 44 Pa chifukwa chimenechi, nanunso khalani okonzeka,+ chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.
45 “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru+ amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?+ 46 Kapolo ameneyu adzakhala wodala+ ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo! 47 Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse.+
48 “Koma ngati kapolo woipayo anganene mumtima mwake+ kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa,’+ 49 n’kuyamba kumenya akapolo anzake ndi kudya komanso kumwa limodzi ndi zidakwa zenizeni, 50 mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera ndi pa ola+ limene sakulidziwa. 51 Pamenepo adzam’patsa chilango choopsa+ ndipo adzam’ponya kumene kuli anthu onyenga. Kumeneko ndiye kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.+
25 “Ufumu wakumwamba udzakhala ngati anamwali 10 amene anatenga nyale+ zawo n’kupita kukachingamira mkwati.+ 2 Anamwali asanu anali opusa,+ ndipo asanu anali ochenjera.+ 3 Pakuti opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta owonjezera. 4 Koma ochenjerawo anatenga mafuta owonjezera m’mabotolo awo limodzi ndi nyale zawo. 5 Popeza kuti mkwati anali kuchedwa, onse anayamba kuwodzera kenako anagona.+ 6 Pakati pa usiku kunamveka mawu ofuula akuti,+ ‘Mkwati uja wafika! Tulukani mukam’chingamire.’ 7 Nthawi yomweyo anamwali onsewo anadzuka ndi kukonza nyale+ zawo. 8 Opusa aja anauza ochenjera kuti, ‘Tigawireniko mafuta+ anu, chifukwa nyale zathu zatsala pang’ono kuzima.’ 9 Ochenjerawo+ anayankha kuti, ‘Mwina satikwanira tikagawana ndi inu. Pitani kwa ogulitsa kuti mukagule anu.’ 10 Atanyamuka kupita kukagula, mkwati anafika, ndipo anamwali okonzekerawo analowa naye limodzi m’nyumba imene munali phwando laukwati,+ ndipo chitseko chinatsekedwa. 11 Pambuyo pake anamwali ena aja nawonso anafika n’kunena kuti, ‘Ambuye, ambuye, titsegulireni!’+ 12 Poyankha iye anati, ‘Kunena zoona, sindikukudziwani inu.’+
13 “Chotero khalanibe maso+ chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.+
14 “Pakuti zili ngati munthu+ amene anali kupita kudziko lina,+ ndipo anaitanitsa akapolo ake ndi kuwasungitsa chuma chake.+ 15 Woyamba anam’patsa ndalama zokwana matalente asanu, wachiwiri anam’patsa matalente awiri, ndipo wachitatu anam’patsa talente imodzi. Aliyense anam’patsa malinga ndi luso lake,+ ndipo iye anapita kudziko lina. 16 Nthawi yomweyo amene analandira matalente asanu uja ananyamuka kukachita nawo malonda ndipo anapindula matalente enanso asanu.+ 17 Chimodzimodzinso amene analandira matalente awiri uja, anapindula enanso awiri. 18 Koma amene analandira imodzi yokha uja anapita kukakumba pansi n’kubisa ndalama yasiliva ya mbuye wakeyo.
19 “Patapita nthawi yaitali,+ mbuye wa akapolowo anabwera ndi kuwerengerana nawo ndalama.+ 20 Choncho amene analandira matalente asanu uja anabwera ndi matalente ena owonjezera asanu, n’kunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente asanu koma onani, ndapindula matalente enanso asanu.’+ 21 Mbuye wakeyo anamuyankha kuti, ‘Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe!+ Unakhulupirika+ pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti udziyang’anira zinthu zambiri.+ Sangalala+ limodzi ndi ine mbuye wako.’ 22 Kenako kunabwera kapolo amene analandira matalente awiri uja n’kunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente awiri koma onani, ndapindula matalente enanso awiri.’+ 23 Mbuye wake anamuyankha kuti, ‘Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe! Unakhulupirika pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri.+ Sangalala+ limodzi ndi ine mbuye wako.’
24 “Pa mapeto pake kunabwera kapolo amene analandira talente imodzi uja,+ ndipo anati, ‘Ambuye, ndinadziwa kuti inu ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese, ndipo mumatuta tirigu kumene simunapete. 25 Choncho ndinachita mantha+ ndipo ndinapita kukabisa talente yanu ija pansi. Nayi ndalama yanu, landirani.’ 26 Poyankha mbuye wakeyo anati, ‘Kapolo woipa ndi waulesi iwe! Ukuti unali kudziwa kuti ineyo ndimakolola kumene sindinafese ndi kututa tirigu kumene sindinapete? 27 Ndiyetu ukanasungitsa ndalama zanga zasilivazi kwa osunga ndalama, ndipo ine pobwera ndikanalandira ndalama zangazo limodzi ndi chiwongoladzanja chake.+
28 “‘Choncho mulandeni talenteyo mupatse amene ali ndi matalente 10.+ 29 Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala nazo zambiri, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 30 Ponyani kapolo wopanda pake ameneyu kunja kumdima. Kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’+
31 “Mwana wa munthu+ akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse,+ adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero.+ 32 Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye+ ndipo adzalekanitsa+ anthu,+ mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. 33 Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja,+ koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.+
34 “Pamenepo mfumu idzauza a kudzanja lake lamanja kuti, ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate+ wanga. Lowani+ mu ufumu+ umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+ 35 Pakuti ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya.+ Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+ 36 Ndinali wamaliseche+ koma inu munandiveka. Ndinadwala koma inu munandisamalira. Ndinali m’ndende+ koma inu munabwera kudzandiona.’ 37 Pamenepo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye, tinakuonani liti muli wanjala ife n’kukudyetsani, kapena muli waludzu,+ ife n’kukupatsani chakumwa?+ 38 Tinakuonani liti muli mlendo ife n’kukulandirani bwino, kapena muli wamaliseche ife n’kukuvekani? 39 Ndi liti pamene tinakuonani mukudwala kapena muli m’ndende ife n’kudzakuchezerani?’ 40 Koma poyankha mfumuyo+ idzawauza kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale+ anga aang’ono+ awa, munachitira ine amene.’+
41 “Kenako adzauza a kumanzere kwake kuti, ‘Chokani pamaso panga+ inu otembereredwa. Pitani kumoto wosatha+ wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake.+ 42 Pakuti ndinamva njala koma inu simunandipatse chakudya.+ Ndinamva ludzu+ koma inu simunandipatse chakumwa. 43 Ndinali mlendo koma inu simunandilandire bwino. Ndinali wamaliseche koma inu simunandiveke.+ Ndinadwala komanso ndinali m’ndende,+ koma inu simunandisamalire.’ 44 Pamenepo nawonso adzayankha kuti, ‘Ambuye, tinakuonani liti muli wanjala kapena waludzu kapena mlendo kapena wamaliseche kapena mukudwala kapena muli m’ndende ife osakutumikirani?’ 45 Pamenepo iye adzawayankha kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, Popeza simunachitire zimenezo mmodzi wa aang’ono awa,+ simunachitirenso+ ine.’+ 46 Ndipo iwowa adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu,+ koma olungama ku moyo wosatha.”+
26 Tsopano Yesu atatsiriza kunena mawu onsewa, anauza ophunzira ake kuti: 2 “Inu mukudziwa kuti pasika achitika pakangopita masiku awiri,+ ndipo Mwana wa munthu aperekedwa kuti akapachikidwe.”+
3 Pa nthawiyi, ansembe aakulu ndiponso akulu anasonkhana m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe wotchedwa Kayafa.+ 4 Iwo anali kupangana+ zoti agwire Yesu mochenjera ndi kumupha. 5 Koma anali kumangonena kuti: “Tisadzamugwire pa chikondwerero, kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.”+
6 Pamene Yesu anali ku Betaniya+ m’nyumba ya Simoni wakhate,+ 7 kunafika mayi wina ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala muli mafuta onunkhira okwera mtengo.+ Mayiyo atayandikira Yesu, anayamba kumuthira mafutawo m’mutu pamene iye anali kudya patebulo. 8 Ophunzira ake ataona zimenezi anakwiya n’kunena kuti: “N’kuwonongeranji chonchi?+ 9 Mafuta amenewa akanagulitsidwa ndalama zambiri ndipo ndalamazo zikanaperekedwa kwa anthu osauka.”+ 10 Yesu anadziwa zimenezi,+ ndipo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino.+ 11 Osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+ 12 Pakuti pamene mayiyu wathira mafuta onunkhirawa pathupi langa chonchi, wachita zimenezi kukonzekera kuikidwa kwanga m’manda.+ 13 Ndithu ndikukuuzani, Kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwe m’dziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzam’kumbukira.”+
14 Pambuyo pake mmodzi wa ophunzira 12 aja, wotchedwa Yudasi Isikariyoti,+ anapita kwa ansembe aakulu 15 n’kuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?”+ Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.+ 16 Choncho kuchokera pamenepo anayesetsa kufunafuna mpata wabwino umene angamuperekere.+
17 Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako pasika?”+ 18 Iye anati: “Pitani mumzinda kwa Munthu wakutiwakuti+ ndipo mukamuuze kuti, Mphunzitsi wanena kuti, ‘Nthawi yanga yoikidwiratu yayandikira. Ndidzachita phwando la pasika pamodzi ndi ophunzira anga kunyumba kwako.’”+ 19 Chotero ophunzirawo anachitadi monga mmene Yesu anawalamulira, ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa pasika.+
20 Nthawi yamadzulo,+ iye ndi ophunzira ake 12 aja anali kudya chakudya patebulo.+ 21 Pamene anali kudya, iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, Mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi zimenezi, aliyense anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?”+ 23 Poyankha iye anati: “Amene akusunsa nane limodzi m’mbalemu ndi amene ati andipereke.+ 24 Zoona, Mwana wa munthu akuchokadi, monga Malemba amanenera+ za iye, koma tsoka+ kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu!+ Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.” 25 Poyankha, Yudasi amene anali atatsala pang’ono kumupereka anati: “Nanga n’kukhala ine Rabi?” Iye anati: “Wanena wekha.”
26 Pamene anali kudya, Yesu anatenga mkate,+ ndipo atapempha dalitso, anaunyemanyema+ n’kuupereka kwa ophunzira ake. Iye anati: “Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 27 Kenako anatenga kapu+ ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo n’kunena kuti: “Imwani nonsenu.+ 28 Vinyoyu akuimira+ ‘magazi+ anga a pangano,’+ amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri+ kuti machimo akhululukidwe.+ 29 Koma ndikukuuzani kuti, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa ichi chochokera ku mphesa kufikira tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano limodzi ndi inu mu ufumu wa Atate wanga.”+ 30 Potsirizira pake, atatha kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,+ anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.+
31 Kenako Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno, pakuti Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa, ndipo nkhosa za m’gululo zidzabalalika.’+ 32 Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.”+ 33 Koma Petulo anamuyankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!”+ 34 Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza iwe, Usiku womwe uno tambala asanalire, undikana katatu.”+ 35 Petulo anayankha kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ophunzira ena onse ananenanso chimodzimodzi.+
36 Kenako Yesu anafika nawo pamalo+ otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzirawo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.”+ 37 Popita kumeneko anatenga Petulo ndi ana awiri+ a Zebedayo. Ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika kwambiri mumtima mwake.+ 38 Kenako anawauza kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho.+ Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”+ 39 Choncho atapita patsogolo pang’ono, anagwada mpaka nkhope yake pansi, ndipo anapemphera+ kuti: “Atate wanga, ngati n’kotheka, kapu+ iyi indipitirire. Koma osati mwa kufuna kwanga,+ koma mwa kufuna kwanu.”+
40 Atatero anabwerera pamene panali ophunzira ake aja ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Zoona anthu inu simungathe kukhalabe maso limodzi ndi ine ola limodzi?+ 41 Khalani maso+ ndipo pempherani+ kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 42 Anachokanso kachiwiri+ n’kupita kukapemphera kuti: “Atate wanga, ngati sizingatheke kuti kapuyi indipitirire mpaka nditamwa ndithu, chifuniro chanu chichitike.”+ 43 Anabwerera n’kuwapezanso akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera.+ 44 Choncho anawasiya ndi kupitanso kukapemphera kachitatu,+ kubwereza mawu omwe aja. 45 Pambuyo pake anabwerera kwa ophunzirawo n’kuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula! Taonani! Ola lakuti Mwana wa munthu aperekedwe m’manja mwa ochimwa layandikira.+ 46 Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+ 47 Mawu adakali m’kamwa, Yudasi,+ mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi khamu lalikulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi kwa akulu, atanyamula malupanga+ ndi zibonga.+
48 Apa n’kuti womupereka ameneyu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndim’psompsone ndi ameneyo, mum’gwire.”+ 49 Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu n’kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu Rabi!”+ Ndipo anam’psompsona.+ 50 Koma Yesu+ anamufunsa kuti: “Bwanawe, ukupezeka kuno ndi cholinga chotani?” Nthawi yomweyo iwo anayandikira ndipo anagwira Yesu ndi kum’manga.+ 51 Koma wina mwa amene anali ndi Yesu anasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 52 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake,+ pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.+ 53 Kapena ukuganiza kuti sindingapemphe Atate wanga kuti anditumizire magulu ankhondo oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino?+ 54 Koma ndikachita zimenezo, nanga Malemba amene ananeneratu kuti izi ziyenera kuchitika adzakwaniritsidwa bwanji?” 55 Mu ola lomwelo Yesu anafunsa khamu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba?+ Tsiku ndi tsiku ndinali kukhala pansi m’kachisi+ ndi kuphunzitsa, koma simunandigwire. 56 Koma zonsezi zachitika kuti malemba a aneneri akwaniritsidwe.”+ Kenako ophunzira ake onse anamuthawa, n’kumusiya yekha.+
57 Amene anagwira Yesu aja anapita naye kwa Kayafa+ mkulu wa ansembe, kumene alembi ndi akulu anali atasonkhana.+ 58 Koma Petulo anali kumutsatirabe chapatali ndithu, mpaka anafika m’bwalo lamkati+ kunyumba ya mkulu wa ansembeyo. Atalowa mkatimo, anakhala pansi pamodzi ndi antchito a m’nyumbamo kuti aone zotsatira zake.+
59 Pa nthawiyi ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* anali kufunafuna umboni wonama kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha+ 60 koma sanaupeze, ngakhale kuti kunabwera mboni zambiri zonama.+ Patapita nthawi, kunabwera mboni zina ziwiri 61 ndi kunena kuti: “Munthu ameneyu ananena kuti, ‘Ndikhoza kugwetsa kachisi wa Mulungu ndi kumumanganso m’masiku atatu.’”+ 62 Pamenepo mkulu wa ansembe anaimirira ndi kumufunsa kuti: “Kodi ukusowa choyankha? Kodi n’zoona zimene awa akukunenezazi?”+ 63 Koma Yesu anangokhala chete.+ Chotero mkulu wa ansembe anati: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo,+ utiuze ngati ndiwedi Khristu+ Mwana wa Mulungu!” 64 Yesu anamuyankha+ kuti: “Mwanena nokha.+ Ndipo ndikukuuzani anthu inu kuti, kuyambira tsopano+ mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera pamitambo yakumwamba.”+ 65 Pamenepo mkulu wa ansembe anang’amba malaya ake akunja n’kunena kuti: “Wanyoza Mulungu!+ Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa?+ Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu.+ 66 Tsopano inu mukuona bwanji pamenepa?” Iwo anayankha kuti: “Ayenera kuphedwa basi.”+ 67 Kenako anayamba kumulavulira kunkhope+ ndi kum’menya+ nkhonya. Ena anamuwomba mbama,+ 68 ndi kunena kuti: “Losera tione Khristu iwe.+ Wakumenya ndani?”+
69 Tsopano Petulo anakhala pansi m’bwalo lamkati, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye n’kunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu wa ku Galileyayu!”+ 70 Koma iye anakana pamaso pa onse kuti: “Sindikudziwa zimene ukunena.” 71 Atatuluka n’kupita kukanyumba kapachipata, mtsikana wina anamuzindikira ndi kuuza ena amene anali pafupi kuti: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu Mnazaretiyu.”+ 72 Apanso Petulo anakana mochita kulumbira ndipo ananena kuti: “Ndithudi munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!”+ 73 Patapita kanthawi pang’ono, amene anali ataimirira chapafupi anabwera ndi kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake. Ndipo kalankhulidwe kako kakugwiritsa.”+ 74 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira kuti: “Munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” Nthawi yomweyo tambala analira.+ 75 Tsopano Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja, akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.”+ Ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.+
27 M’mawa kutacha, ansembe aakulu limodzi ndi akulu onse anakambirana ndi kugwirizana kuti aphe Yesu.+ 2 Ndipo atam’manga, anapita kukam’pereka kwa bwanamkubwa Pilato.+
3 Pamenepo Yudasi amene anam’pereka uja ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti aphedwe, anavutika koopsa mumtima mwake moti anapita kukabweza ndalama 30+ zasiliva zija kwa ansembe aakulu ndiponso akulu. 4 Iye anati: “Ndachimwa popereka munthu wolungama.”*+ Koma iwo anamuyankha kuti: “Ife sizikutikhudza zimenezo. Udziwa wekha chochita!”+ 5 Choncho iye anaponya ndalama zasiliva zija m’kachisi n’kuchoka, ndipo anakadzimangirira.+ 6 Koma ansembe aakulu anatenga ndalama zasilivazo n’kunena kuti: “N’kosaloleka kuponya ndalamazi m’malo opatulika osungiramo chuma, chifukwa ndi malipiro a magazi.” 7 Koma atakambirana, anatenga ndalamazo n’kukagulira munda wa woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo. 8 Choncho munda umenewu umatchedwa “Munda wa Magazi”+ mpaka lero. 9 Pamenepo zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yeremiya* zinakwaniritsidwa. Iye anati: “Ndipo anatenga ndalama 30 zasiliva,+ zomwe zinali mtengo wogulira munthu umene ena mwa ana a Isiraeli anamuikira, 10 ndipo anagulira munda wa woumba mbiya,+ malinga ndi zimene Yehova anandilamula.”
11 Tsopano Yesu anaimirira pamaso pa bwanamkubwa, ndipo bwanamkubwayo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?”+ Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha.”+ 12 Koma pamene ansembe aakulu komanso akulu anali kumuneneza,+ iye sanayankhe chilichonse.+ 13 Pamenepo Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sukumva zonse zimene akukunenezazi?”+ 14 Koma iye anangokhala duu, osanena kanthu, moti bwanamkubwayo anadabwa kwambiri.+
15 Pa chikondwerero chilichonse, bwanamkubwayu anali ndi dongosolo lomasulira anthu mkaidi mmodzi amene anthuwo akufuna.+ 16 Ndipo pa nthawiyi panali mkaidi wina wowopsa kwambiri wotchedwa Baraba.+ 17 Choncho atasonkhana pamodzi, Pilato ananena kuti: “Kodi mukufuna ndikumasulireni ndani, Baraba kapena Yesu, uja amamuti Khristu?”+ 18 Pakuti iye anadziwa kuti anamupereka chifukwa cha kaduka.+ 19 Komanso atakhala pampando woweruzira milandu, mkazi wake anamutumizira mawu akuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni.+ Inetu ndavutika kwambiri lero m’maloto+ chifukwa cha iyeyu.” 20 Koma ansembe aakulu limodzi ndi akulu analimbikitsa anthu kupempha kuti awamasulire Baraba,+ ndi kuti Yesu aphedwe. 21 Pamenepo bwanamkubwayo anawafunsa kuti: “Ndani mwa awiriwa amene mukufuna kuti ndikumasulireni?” Iwo anati: “Baraba.”+ 22 Pilato anafunsanso kuti: “Nanga Yesu, uja amamuti Khristu, ndichite naye chiyani?” Onse anayankha kuti: “Apachikidwe ameneyo!”+ 23 Iye anati: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma atatero m’pamene anawonjezera kufuula kuti: “Apachikidwe basi!”+
24 Poona kuti sizikuthandiza, komanso pakuyambika chipolowe, Pilato anangotenga madzi+ ndi kusamba m’manja pamaso pa khamu la anthulo, n’kunena kuti: “Inetu ndasamba m’manja, ndilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.” 25 Atanena izi anthu onse anayankha kuti: “Magazi ake akhala pa ife ndi pa ana athu.”+ 26 Pamenepo anawamasulira Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe+ kenako anamupereka kuti akam’pachike.+
27 Ndiyeno asilikali a bwanamkubwa anatengera Yesu m’nyumba ya bwanamkubwa n’kusonkhanitsa khamu lonse la asilikali kwa iye.+ 28 Kumeneko anamuvula zovala zake ndi kumuveka chinsalu chofiira kwambiri.+ 29 Komanso analuka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka kumutu n’kumupatsa bango m’dzanja lake lamanja. Kenako anamugwadira ndi kum’chitira zachipongwe+ kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!”+ 30 Atatero anamulavulira+ ndi kutenga bango lija ndi kuyamba kum’menya nalo m’mutu. 31 Atamaliza kumuchitira zachipongwezo,+ anamuvula chinsalu chija ndi kumuveka malaya ake akunja n’kupita naye kukamupachika.+
32 Pamene anali kupita, anakumana ndi Simoni, nzika ya ku Kurene.+ Iwo anasenzetsa munthu ameneyu mtengo wozunzikirapo* wa Yesu. 33 Atafika pamalo otchedwa Gologota,+ kutanthauza kuti, Malo a Chibade, 34 anapatsa Yesu vinyo wosakaniza ndi ndulu+ kuti amwe, koma iye atalawa, anakana kumwa.+ 35 Atam’pachika+ anagawana malaya ake akunja+ mwa kuchita maere,+ 36 ndipo anakhala pansi n’kumamuyang’anira. 37 Komanso pamwamba pa mutu wake anakhomapo chikwangwani cha mawu osonyeza mlandu wake kuti: “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.”+
38 Achifwamba awiri anapachikidwa limodzi ndi iye, mmodzi kudzanja lake lamanja, wina kumanzere kwake.+ 39 Tsopano anthu odutsa anayamba kunena mawu onyoza+ Yesu. Anali kupukusa+ mitu yawo 40 n’kumanena kuti: “Iwe wogwetsa kachisi+ ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikirapowo!”+ 41 Chimodzimodzinso ansembe aakulu limodzi ndi alembi komanso akulu. Nawonso anayamba kum’chita chipongwe ndi kunena kuti:+ 42 “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ameneyutu ndi Mfumu+ ya Isiraeli, atsiketu pamtengo wozunzikirapowo kuti ife timukhulupirire.+ 43 Suja amakhulupirira Mulungu? Mulunguyo am’pulumutse+ tsopano ngati akumufunadi. Ndi ujatu anali kunena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’”+ 44 Nawonso achifwamba amene anapachikidwa naye limodzi anayamba kumunyoza.+
45 Kuyambira cha m’ma 12 koloko masana* kunagwa mdima+ m’dziko lonselo, mpaka 3 koloko masana.*+ 46 Cha m’ma 3 kolokomo Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+ 47 Atamva izi, ena mwa anthu amene anaimirira chapomwepo anayamba kunena kuti: “Munthuyu akuitana Eliya.”+ 48 Nthawi yomweyo mmodzi wa iwo anathamanga kukatenga chinkhupule ndi kuchiviika m’vinyo wowawasa+ ndipo anachiika kubango ndi kum’patsa kuti amwe.+ 49 Koma enawo anati: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzam’pulumutsa.”+ [[Munthu wina anatenga mkondo ndi kumubaya* m’mbalimu cham’mimba ndipo panatuluka magazi ndi madzi.]]*+ 50 Pamenepo Yesu anafuulanso mokweza mawu, kenako anatsirizika.+
51 Nthawi yomweyo nsalu yotchinga+ ya m’nyumba yopatulika inang’ambika pakati kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ Dziko lapansi linagwedezeka, ndipo matanthwe anang’ambika.+ 52 Manda achikumbutso anatseguka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera amene anaikidwa mmenemo inaponyedwa kunja, 53 ndi kuonekera kwa anthu ambiri. (Pambuyo pa kuukitsidwa kwa Yesu, anthu amene anali kuchokera kumanda achikumbutsoko, analowa mumzinda woyera.)+ 54 Koma kapitawo wa asilikali ndi ena amene anali naye polondera Yesu ataona chivomezicho ndi zimene zimachitikazo, anachita mantha kwambiri ndipo anati: “Ndithudi, uyu analidi Mwana wa Mulungu.”+
55 Komanso akazi ambiri ochokera ku Galileya amene ankatsatira Yesu kuti azimutumikira,+ anali komweko akuonerera chapatali ndithu.+ 56 Pakati pawo panali Mariya Mmagadala, Mariya mayi a Yakobo ndi Yose, ndiponso panali mayi a Yakobo ndi Yohane.*+
57 Tsopano madzulo, munthu wina wachuma wa ku Arimateya, wotchedwa Yosefe, amenenso anakhala wophunzira wa Yesu,+ 58 anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.+ Pilato analamula kuti amupatse mtembowo.+ 59 Yosefe anatenga mtembowo ndi kuukulunga munsalu yoyera yabwino kwambiri,+ 60 ndipo anakauika m’manda ake achikumbutso atsopano,+ amene anawasema m’thanthwe. Kenako anagubuduza chimwala chachikulu ndi kutseka pakhomo la manda achikumbutsowo, n’kuchoka.+ 61 Koma Mariya Mmagadala ndi Mariya wina anatsalira komweko, atakhala pansi pafupi ndi mandawo.+
62 Tsiku lotsatira, pambuyo pa Tsiku Lokonzekera,+ ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana pamaso pa Pilato, 63 ndi kunena kuti: “Bwana, ife takumbukira kuti wonyenga uja adakali moyo ananena kuti, ‘Patapita masiku atatu ndidzauka.’+ 64 Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo kufikira tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba+ ndi kuuza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ pakuti chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.” 65 Pilato anawayankha kuti: “Inu muli nawo asilikali olondera.+ Pitani kakhwimitseni chitetezo monga mmene mukudziwira.” 66 Choncho anapita ndi kukakhwimitsa chitetezo pamandawo mwa kutseka kwambiri mandawo ndi chimwala*+ n’kuikapo asilikali olondera.
28 Tsiku la sabata litatha, m’bandakucha wa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya Mmagadala ndi Mariya wina uja anabwera kudzaona manda.+
2 Atafika pafupi, anazindikira kuti pachitika chivomezi champhamvu, pakuti mngelo wa Yehova anatsika kumwamba, ndipo anafika ndi kugubuduza chimwala chija, n’kukhala pachimwalapo.+ 3 Maonekedwe ake anali ngati a mphezi,+ ndipo zovala zake zinali zoyera mbee!+ 4 Alonda aja pochita mantha ndi mngeloyo, ananjenjemera ndipo anangouma gwaa ngati akufa.
5 Koma mngeloyo+ anauza amayiwo kuti: “Inu musachite mantha, chifukwa ndikudziwa kuti mukufuna Yesu+ amene anapachikidwa. 6 Iye sali pano chifukwa wauka kwa akufa+ monga ananenera. Bwerani muone pamene anagona. 7 Ndipo pitani mwamsanga mukauze ophunzira ake kuti wauka kwa akufa,+ moti padakali pano, watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona. Umenewutu ndi uthenga wanga kwa inu.”+
8 Choncho, iwo anachoka mwamsanga pamanda achikumbutsowo, ali ndi mantha ndiponso chimwemwe chochuluka, ndipo anathamanga kukauza ophunzira ake.+ 9 Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo n’kunena kuti: “Moni amayi!” Pamenepo iwo anafika pafupi ndi kugwira mapazi ake ndi kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi. 10 Kenako Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga,+ kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.”
11 Adakali m’njira, alonda+ ena anapita mumzinda ndipo anakauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitika. 12 Ansembe aakuluwo atakambirana ndi akulu, anapangana zochita ndipo anapereka ndalama zasiliva zambiri kwa asilikaliwo+ 13 n’kuwauza kuti: “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake+ anabwera usiku kudzamuba ife titagona.’ 14 Bwanamkubwa akamva zimenezi, tikamunyengerera ndipo inu musade naye nkhawa.” 15 Choncho anatenga ndalama zasilivazo ndi kuchita monga anawauzira ndipo nkhani imeneyi inafala kwambiri pakati pa Ayuda mpaka lero.
16 Koma ophunzira 11 aja anapita ku Galileya,+ kuphiri kumene Yesu anakonza kukakumana nawo. 17 Atamuona anamugwadira, koma ena anakayika ngati anali iye.+ 18 Tsopano Yesu anayandikira ndi kulankhula nawo kuti: “Ulamuliro wonse+ waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi. 19 Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse+ kuti akhale ophunzira anga.+ Muziwabatiza+ m’dzina la Atate,+ ndi la Mwana,+ ndi la mzimu woyera,+ 20 ndi kuwaphunzitsa+ kusunga+ zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.+ Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu+ masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi* ino.”+
Mawu ake enieni, “anaganiza zothetsa ukwati mwamseri.” Pa mwambo wachiyuda, kuti lonjezo loti anthu adzakwatirana lithe ankatsatira dongosolo lothetsera ukwati.
Onani Zakumapeto 2.
Pa Chiheberi dzinali amati “Yesuwa,” ndipo limatanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso.”
Ameneyu anali Herode Wamkulu.
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani Zakumapeto 2.
M’Baibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete, komanso nyanja ya Tiberiyo.
Onani Zakumapeto 6.
Mawu ake enieni, “limakupunthwitsa.”
Onani Zakumapeto 7.
Mawu ake enieni, “ngongole.”
Mawu ake enieni, “ali nafe ngongole.”
Mawu amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
Mawu ake enieni, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.”
Kapena kuti “tsindwi.”
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
“Petulo” amatchedwa ndi mayina asanu. Pano akutchedwa “Simoni, wotchedwa Petulo.” Pa Mt 16:16 akutchedwa “Simoni Petulo,” pa Mac 15:14, “Sumeoni,” ndipo pa Yoh 1:42, “Kefa.” Koma nthawi zambiri amatchedwa “Petulo,” monga mmene zilili pa Mt 14:28.
Dzina lakuti “Kananiya” likutanthauza munthu wachangu.
“Belezebule” ndi dzina lina la Satana.
Onani Zakumapeto 6.
Onani Zakumapeto 9.
Ena amati “masaka.”
Onani Zakumapeto 5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakang’ono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita anayi ndipo kamachita nthambi.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ameneyu anali Herode Antipa, mwana wa Herode Wamkulu.
Mu nthawi ya Aroma, Ayuda ankagawa usiku m’magawo anayi. Chigawo choyamba chinali kuyamba 6 koloko madzulo mpaka 9 koloko usiku. Chigawo chachiwiri chinali kuyamba 9 koloko mpaka 12 koloko usiku. Chigawo chachitatu chinali kuyamba 12 koloko usiku mpaka 3 koloko ndipo chigawo chachinayi chinali kuyamba 3 koloko mpaka 6 koloko m’mawa.
Izi sizikutanthauza kuti anali kudya ndi m’manja mwakuda, koma kuti sanali kutsatira miyambo yachiyuda yosambira m’manja.
Mikutiramawu yophatikiza ikusonyeza mawu amene m’mipukutu ina yakale mulibe koma akupezeka m’mipukutu ina.
Mawu ake enieni, “mnofu ndi magazi.”
Onani Zakumapeto 9.
Mawu a vesi limeneli akupezeka m’Mabaibulo ena, koma mulibemo m’Baibulo lachigiriki la Westcott ndi Hort limene limagwirizana ndi mipukutu yakale kwambiri yachigiriki.
Mawu ake enieni “khobidi la siteta.” Khobidi limeneli linali lofanana ndi madalakima anayi.
Onani Zakumapeto 6.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Onani Zakumapeto 7.
Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
Mawu ake enieni, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 6 ndi ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 11,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 2.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Onani Zakumapeto 6.
Kutanthauza kachisi.
Onani Zakumapeto 8.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”
Mawu ake enieni, “magazi olungama.”
Mawuwa kwenikweni ndi a pa Zek 11:12, 13. M’nthawi ya Mateyu, buku la Yeremiya linali loyambirira mumpukutu wa mabuku a aneneri. Chotero mwina mabuku onsewo a aneneri, kuphatikizapo la Zekariya, anali kutchedwa kuti Yeremiya. Yerekezani ndi Lu 24:44.
Onani Zakumapeto 9.
Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Ena amati “kugwaza.”
Onani mawu a m’munsi pa Mt 16:3.
Mawu ake enieni, “mayi wa ana a Zebedayo.”
Mawu achigiriki amanena kuti mwalawo anauchita zinazake kuti ngati wina atausuntha iwo adzadziwe.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.