Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Zechariah 1:1-14:21
  • Zekariya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zekariya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Zekariya

Zekariya

1 M’mwezi wa 8, m’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya,+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido,+ kuti: 2 “Yehova anakwiyira kwambiri makolo anu.+

3 “Uwauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “‘Bwererani kwa ine,’+ watero Yehova wa makamu, ‘ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,’+ akutero Yehova wa makamu.”’

4 “‘Musakhale ngati makolo anu+ amene aneneri akale anawauza mofuula+ kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndi zochita zanu zoipa n’kubwerera kwa ine!’”’+

“‘Koma iwo sanamvere ndipo sanalabadire mawu anga,’+ watero Yehova.

5 “‘Kodi makolo anuwo ali kuti?+ Ndipo “kodi aneneriwo+ anapitirizabe kukhala ndi moyo mpaka kalekale?”* 6 Kodi zimene ndinalamula atumiki anga aneneri+ m’mawu anga ndi m’malangizo anga, sizinawachitikire makolo anu?’+ Chotero iwo anabwerera kwa ine ndi kunena kuti: ‘Yehova wa makamu watichitira zimene anakonza kuti atichitire+ mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+

7 Pa tsiku la 24, m’mwezi wa 11 womwe ndi mwezi wa Sebati, m’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova anaonetsa masomphenya mneneri Zekariya,+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido.+ Masomphenya amene ndinaonawo ndi awa: 8 “Unali usiku pamene ndinaona munthu+ atakwera pahatchi* yofiira.+ Iye anaima chilili pakati pa mitengo ya mchisu+ imene inali m’chigwa. Kumbuyo kwake kunali mahatchi ofiirira, ofiira kwambiri ndi oyera.”+

9 Choncho, ine ndinafunsa kuti: “Kodi amenewa ndani mbuyanga?”+

Pamenepo mngelo amene anali kulankhula nane anandiyankha+ kuti: “Ine ndikuuza za amenewa.”

10 Kenako munthu amene anaima chilili pakati pa mitengo ya mchisu uja anayankha kuti: “Amenewa atumizidwa ndi Yehova kuti ayendeyende padziko lapansi.”+ 11 Ndiyeno iwo anauza mngelo wa Yehova amene anaima chilili pakati pa mitengo ya mchisu uja kuti: “Ife tayendayenda padziko lapansi+ ndipo taona kuti dziko lonse lapansi langokhala bata popanda chosokoneza.”+

12 Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa makamu, kodi Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda imene munaikana ndi kuisiya kwa zaka 70,+ simuichitira chifundo kufikira liti?”+

13 Yehova anayankha mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja. Anamuyankha ndi mawu abwino ndiponso olimbikitsa.+ 14 Ndiyeno mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja anandiuza kuti: “Fuula kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ndakhala ndikuchitira nsanje kwambiri Yerusalemu ndi Ziyoni.+ 15 Ndakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene akukhala mwabata.+ Ndawakwiyira chifukwa chakuti ine ndinangokwiyira anthu anga pang’ono pokha,+ koma anthu amenewa anakulitsa tsoka la anthu angawo.”’+

16 “Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndithu ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi kuchitira chifundo mzinda umenewu.+ Nyumba yanga idzamangidwa mmenemo,+ ndipo chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa makamu.’

17 “Fuulanso kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mizinda yanga idzasefukira ndi zinthu zabwino.+ Yehova adzamva chisoni chifukwa cha tsoka limene anagwetsera Ziyoni+ ndipo adzasankhanso Yerusalemu.”’”+

18 Kenako ndinaona nyanga zinayi m’masomphenya.+ 19 Choncho ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula nane uja kuti: “Kodi nyangazi zikutanthauza chiyani?” Iye anandiyankha kuti: “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda,+ Isiraeli+ ndi Yerusalemu.”+

20 Yehova anandionetsanso amisiri anayi. 21 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Kodi awa abwera kudzachita chiyani?”

Mngeloyo anayankha kuti: “Zimenezi ndi nyanga+ zimene zinabalalitsa Yuda, moti panalibe amene anatha kudzutsa mutu wake. Amisiri awa adzabwera kudzaopseza nyangazi, kudzawononga nyanga za mitundu ina ya anthu imene ikukwezera nyanga* yawo dziko la Yuda kuti ibalalitse anthu ake.”+

2 Tsopano ndinakweza maso ndipo ndinaona munthu ali ndi chingwe choyezera m’dzanja lake.+ 2 Ndiyeno ndinam’funsa kuti: “Ukupita kuti?”

Iye anandiyankha kuti: “Ndikupita kukayeza Yerusalemu kuti ndidziwe kutalika kwa m’litali mwake ndi m’lifupi mwake.”+

3 Pamenepo mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja ananyamuka n’kumapita, ndipo kunabwera mngelo wina kudzakumana naye. 4 Mngeloyo anauza mnzakeyo kuti: “Thamanga ukauze mnyamata uyo kuti, ‘“Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati mudzi wopanda mpanda+ chifukwa cha kuchuluka kwa anthu ndi ziweto zimene zili mmenemo.+ 5 Ine ndidzamuzungulira ngati mpanda wake wamoto+ ndipo ndidzamudzaza ndi ulemerero wanga,”’ watero Yehova.”+

6 “Fulumirani! Fulumirani anthu inu! Thawani m’dziko la kumpoto,”+ watero Yehova.

“Anthu inu, ndinakubalalitsirani kutali kumbali zonse za dziko lapansi,”*+ watero Yehova.

7 “Fulumira Ziyoni!+ Thawa, iwe amene ukukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.+ 8 Pambuyo popatsidwa ulemerero,+ Mulungu wandituma kwa anthu a mitundu ina amene anali kukulandani zinthu zanu,+ pakuti Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Amene akukukhudzani,+ akukhudza mwana wa diso langa.+ 9 Ine ndikuwaloza mowaopseza,+ ndipo adzatengedwa ndi akapolo awo kuti akhale chuma cha akapolowo.’+ Ndithu, anthu inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma.+

10 “Fuula kwambiri ndi kusangalala, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,+ pakuti ine ndikubwera+ ndipo ndidzakhala mwa iwe,”+ watero Yehova. 11 “Mitundu yambiri ya anthu idzadziphatika kwa Yehova pa tsikulo,+ choncho adzakhala anthu anga.+ Ine ndidzakhala mwa iwe.” Ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa iwe.+ 12 Yehova adzatenga Yuda kukhala gawo lake m’dziko loyera,+ ndipo adzasankha Yerusalemu.+ 13 Anthu nonsenu, khalani chete pamaso pa Yehova,+ pakuti iye wanyamuka+ m’malo ake oyera okhalamo.+

3 Ndiyeno Mulungu anandionetsa Yoswa+ mkulu wa ansembe, ataimirira pamaso pa mngelo wa Yehova. Pa nthawiyi Satana+ anali ataimirira kudzanja lamanja la Yoswa kuti azim’tsutsa.+ 2 Kenako mngelo+ wa Yehova anauza Satana kuti: “Iwe Satana, Yehova akudzudzule!+ Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzule!+ Kodi munthu uyu si chikuni chimene chaphulidwa pamoto msangamsanga?”+

3 Pa nthawi imene Yoswa anaimirira pamaso pa mngelo, anali atavala zovala zonyansa.+ 4 Ndiyeno mngeloyo anauza amene anaimirira pamaso pake kuti: “Muvuleni zovala zonyansazi.” Kenako anauza Yoswa kuti: “Waona, ndakuchotsera zolakwa zako,+ ndipo wavekedwa mikanjo yapadera.”+

5 Pamenepo ndinanena kuti: “Auzeni kuti amuveke nduwira* yoyera kumutu kwake.”+ Ndipo anamuvekadi nduwira yoyera kumutu kwake. Anamuvekanso zovala. Apa n’kuti mngelo wa Yehova ataimirira pambali pake. 6 Mngelo wa Yehova uja anayamba kulimbikitsa Yoswa kuti: 7 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ukayenda m’njira zanga ndi kusunga malamulo anga,+ udzakhala woweruza wa anthu a m’nyumba yanga+ ndipo uzidzayang’anira mabwalo a nyumba yanga. Ndithu ndidzakulola kumafika pamaso panga limodzi ndi amene aima panowa.’

8 “‘Tamvera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi pamaso pako, pakuti iwo ndi amuna amene ali ngati zizindikiro zolosera zam’tsogolo.+ Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+ 9 Taonani mwala+ umene ndauika pamaso pa Yoswa. Mwala umenewu uli ndi maso 7.+ Pamwalawu ndilembapo zinthu mochita kugoba,+ ndipo ndidzachotsa zolakwa za dzikoli m’tsiku limodzi,’+ watero Yehova wa makamu.

10 “‘Pa tsiku limenelo mudzaitanizana, aliyense atakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndiponso wa mkuyu,’+ watero Yehova wa makamu.”

4 Mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja anabwerera n’kundidzutsa, ndipo ndinadzuka ngati munthu amene anali kugona.+ 2 Kenako anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”+

Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona choikapo nyale chagolide yekhayekha.+ Pamwamba pake pali mbale yolowa. Choikapo nyalecho chili ndi nyale 7, inde, nyale 7.+ Nyale zimene zili pachoikapo nyalecho, zili ndi mapaipi 7. 3 M’mbali mwa choikapo nyalecho muli mitengo iwiri ya maolivi.+ Umodzi uli mbali ya kudzanja lamanja la mbale yolowayo, ndipo wina uli kumanzere kwa mbaleyo.”

4 Kenako ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi zimenezi zikuimira chiyani mbuyanga?”+ 5 Mngeloyo anandiyankha kuti: “Kodi sukudziwadi tanthauzo la zinthu zimenezi?”

Pamenepo ine ndinati: “Inde sindikudziwa mbuyanga.”+

6 Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo,+ kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa makamu. 7 Ngakhale pataikidwa chopinga chachikulu ngati phiri+ pamaso pa Zerubabele,+ chidzasalazidwa kukhala malo athyathyathya. Ndithu iye adzabweretsa mwala wotsiriza wa pakona.+ Akadzatero anthu adzafuula+ kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”+

8 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 9 “Manja a Zerubabele anayala maziko a nyumbayi,+ ndipo manja ake omwewo adzaimalizitsa.+ Pamenepo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.+ 10 Munthu asakunyozeni chifukwa chakuti munayamba kumanga ndi zinthu zochepa.+ Anthu adzasangalala ndi ntchito imeneyi+ ndipo adzaona chingwe cha mmisiri womanga nyumba m’dzanja la Zerubabele. Maso 7 adzaona zimenezi. Maso 7 amenewa ndiwo maso a Yehova,+ ndipo akuyang’ana uku ndi uku padziko lonse lapansi.”+

11 Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi mitengo iwiri ya maolivi, imene wina uli kudzanja lamanja ndi wina kumanzere kwa choikapo nyalechi, ikuimira chiyani?”+ 12 Ndinamufunsanso kuti: “Kodi nthambi ziwiri izi za mitengo ya maolivi, zimene zikuthira mafuta agolide m’mbale yolowa kudzera m’mapaipi awiri agolide, zikuimira chiyani?”

13 Iye anandiyankha kuti: “Kodi sukudziwadi tanthauzo la zinthu zimenezi?”

Pamenepo ine ndinati: “Inde sindikudziwa mbuyanga.”+

14 Ndipo iye anandiuza kuti: “Zinthu zimenezi zikuimira odzozedwa awiri+ amene amaimirira kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.”+

5 Kenako ndinakweza maso anga ndipo ndinaona mpukutu ukuuluka.+ 2 Iye anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”+

Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mpukutu ukuuluka. Mpukutuwo ndi wautali mikono* 20 ndipo m’lifupi mwake ndi wautali mikono 10.”

3 Ndiyeno anandiuza kuti: “Ili ndi temberero limene likubwera padziko lonse lapansi,+ chifukwa aliyense amene akuba+ sakulandira chilango, monga mmene temberero limene lalembedwa kumbali imodzi ya mpukutuwo likunenera. Komanso aliyense amene akulumbira mwachinyengo+ sakulandira chilango, monga mmene temberero limene lalembedwa kumbali inayo ya mpukutuwo likunenera.+ 4 Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndatumiza mpukutuwo kuti ukalowe m’nyumba ya munthu wakuba ndi m’nyumba ya munthu wolumbira mwachinyengo m’dzina langa.+ Mpukutuwo upita kukakhala m’nyumba mwake n’kuwonongeratu nyumbayo, matabwa ake ndi miyala yake.’”+

5 Kenako mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja anandiyandikira n’kundiuza kuti: “Kweza maso ako uone chimene chikubwera.”

6 Choncho ndinafunsa kuti: “N’chiyani chimenechi?”

Iye anandiyankha kuti: “Chimenechi ndi chiwiya choyezera chokwana muyezo wa efa.”* Ndiyeno anapitiriza kunena kuti: “Umu ndi mmene amaonekera anthu oipa a padziko lonse lapansi.” 7 Tsopano chivundikiro chamtovu cha chiwiya choyezeracho chinavundukulidwa, ndipo mkati mwa chiwiyacho, ndinaonamo mkazi atakhala pansi. 8 Mngelo uja anandiuza kuti: “Mkazi ameneyu dzina lake ndi Kuipa.” Kenako anamukankha n’kumubwezera m’chiwiya choyezera chokwana muyezo wa efacho,+ ndipo anavundikira chiwiyacho ndi chivundikiro chake chamtovu chija.

9 Ndiyeno ndinakweza maso ndipo ndinaona akazi awiri akubwera. Akaziwo anali kuuluka ndi mapiko ooneka ngati a dokowe ndipo mphepo inali kuwomba mapikowo. Iwo ananyamula chiwiya choyezera chija n’kupita nacho m’mwamba, pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba. 10 Choncho ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Chiwiya choyezeracho akupita nacho kuti?”

11 Iye anandiyankha kuti: “Akupita nacho kudziko la Sinara+ kuti akamangire+ mkaziyo nyumba kumeneko. Akamumangira nyumba yolimba ndipo akamukhazika kumeneko pamalo ake oyenera.”

6 Ndinakwezanso maso ndipo ndinaona magaleta anayi akubwera kuchokera pakati pa mapiri awiri. Mapiriwo anali amkuwa. 2 Galeta loyamba linali kukokedwa ndi mahatchi ofiira,+ ndipo galeta lachiwiri linali kukokedwa ndi mahatchi akuda.+ 3 Galeta lachitatu linali kukokedwa ndi mahatchi oyera,+ ndipo galeta lachinayi linali kukokedwa ndi mahatchi amawangamawanga.+

4 Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi magaleta amenewa akuimira chiyani mbuyanga?”+

5 Mngeloyo anandiyankha kuti: “Magaletawa akuimira zolengedwa zauzimu zinayi+ zakumwamba zimene zikubwera+ pambuyo poimirira pamaso pa Ambuye+ wa dziko lonse lapansi.+ 6 Mahatchi akuda amene akukoka galeta akupita kudziko la kumpoto.+ Mahatchi oyera akupita kutsidya la nyanja. Mahatchi amawangamawanga akupita kudziko la kum’mwera.+ 7 Mahatchi amawangamawanga+ apitanso kukafufuza koti alowere kuti azikayendayenda mbali ina ya dziko lapansi.”+ Kenako iye anauza mahatchiwo kuti: “Pitani, mukayendeyende padziko lapansi.” Mahatchiwo anapita n’kumakayendayenda padziko lapansi.

8 Mngelo uja anandiitana mofuula n’kundiuza kuti: “Taona, mkwiyo+ umene Yehova anali nawo padziko la kumpoto watha chifukwa cha mahatchi amene apita kumeneko.”+

9 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 10 “Ukalandire chopereka kuchokera kwa anthu amene anatengedwa kupita kudziko lina.+ Ukalandire choperekacho kwa Heledai, Tobiya ndi Yedaya. Iweyo upite pa tsiku loikidwiratu, ndipo ukalowe m’nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya,+ kumene kuli anthu ochokera ku Babulowo. 11 Pa choperekacho ukatengepo siliva ndi golide n’kupangira chisoti chachifumu chaulemerero.+ Chisoticho udzaveke Yoswa+ mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki. 12 Ndiyeno udzamuuze kuti,

“‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Munthu uyu+ dzina lake ndi Mphukira.+ Adzaphuka pamalo ake ndipo adzamanga kachisi wa Yehova.+ 13 Munthu ameneyu adzamanga kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero.+ Iye azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu ndipo adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo.+ Maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana.+ 14 Chisoti chachifumu chaulemererocho chizidzakhala m’kachisi wa Yehova kuti anthu azidzakumbukira+ Helemu, Tobiya, Yedaya+ ndi Heni mwana wa Zefaniya. 15 Anthu amene ali kutali, ndithu adzabwera kudzamanga nawo kachisi wa Yehova.”+ Anthu inu mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu,+ mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.’”+

7 M’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo,+ Yehova analankhula ndi Zekariya pa tsiku lachinayi m’mwezi wa 9, umene ndi mwezi wa Kisilevi.+ 2 Anthu a ku Beteli anatumiza Sarezere ndi Regemu-meleki limodzi ndi anthu ake, kuti akakhazike pansi+ mtima wa Yehova. 3 Anawatuma kuti akauze ansembe+ a panyumba ya Yehova wa makamu ndi aneneri kuti: “Kodi tilire* m’mwezi wachisanu+ ndi kukhala osadya ngati mmene takhala tikuchitira zaka zonsezi?”+

4 Yehova wa makamu anapitiriza kulankhula nane kuti: 5 “Kauze anthu onse a m’dzikoli ndi ansembe kuti, ‘Pamene munali kusala kudya+ ndi kulira m’mwezi wachisanu komanso m’mwezi wa 7+ kwa zaka 70,+ kodi munalidi kusala kudya chifukwa cha ine?+ 6 Pamene munali kudya ndi kumwa, kodi simunali kudya ndi kumwa kuti mudzisangalatse nokha? 7 Kodi simunayenera kumvera mawu+ amene Yehova ananena kudzera mwa aneneri akale,+ pamene mu Yerusalemu ndi mizinda yake yonse yozungulira munali kukhala anthu, komanso pamene munali bata? Kodi simunayenera kumvera Mulungu pamene ku Negebu+ ndi ku Sefela+ kunali kukhala anthu?’”

8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Zekariya kuti: 9 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Muzichita chilungamo chenicheni poweruza milandu.+ Muzisonyezana kukoma mtima kosatha+ ndi chifundo.+ 10 Musamabere mwachinyengo mkazi wamasiye,+ mwana wamasiye,*+ mlendo+ kapena munthu wosautsika.+ Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu.’+ 11 Koma iwo anakanabe kumvetsera.+ Anapitiriza kumulozetsa nkhongo+ ndipo anatseka makutu awo kuti asamve chilichonse.+ 12 Iwo anaumitsa mtima wawo+ ngati mwala wolimba kwambiri kuti asamvere malamulo+ ndi mawu a Yehova wa makamu, amene anawatumizira mwa mzimu wake+ kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa makamu anakwiya kwambiri.”+

13 “‘Popeza kuti ine ndikawaitana sanali kundimvera,+ iwonso akandiitana sindinali kuwamvera,’+ watero Yehova wa makamu. 14 ‘Chotero ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu+ imene sanali kuidziwa,+ ngati kuti atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya labwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kuyendayendamo.+ Iwo anasandutsa dziko losiririka+ kukhala chinthu chodabwitsa.’”

8 Yehova wa makamu anapitiriza kulankhula kuti: 2 “Yehova wa makamu+ wanena kuti: ‘Ziyoni ndidzam’chitira nsanje kwambiri.+ Ndidzam’chitira nsanje ndi kukwiya kwambiri.’”+

3 “Yehova wanena kuti, ‘Ndidzabwerera ku Ziyoni+ ndipo ndidzakhala mu Yerusalemu.+ Yerusalemu adzatchedwadi mzinda wa choonadi+ ndi phiri loyera+ la Yehova+ wa makamu.’”

4 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’bwalo la mzinda wa Yerusalemu mudzakhala amuna ndi akazi achikulire.+ Aliyense adzatenga ndodo+ m’dzanja lake pakuti masiku ake adzakhala atachuluka. 5 M’mabwalo a mzindawo mudzadzaza anyamata ndi atsikana ndipo azidzasewera mmenemo.’”+

6 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ngakhale kuti m’masiku amenewo otsalira a anthu awa adzaona kuti zimenezo n’zosatheka, kodi zidzakhalanso zosatheka kwa ine?’+ watero Yehova wa makamu.”

7 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndipulumutsa anthu anga kuchokera kudziko la kum’mawa ndiponso kuchokera kudziko la kumadzulo.+ 8 Ndithu ndidzawabweretsa, ndipo adzakhala mu Yerusalemu.+ Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo woona ndi wachilungamo.’”+

9 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Limbani mtima anthu inu ndipo mukonzeke kugwira ntchito,+ inu amene mukumva mawu a aneneri masiku ano.+ Awa ndi mawu amene aneneriwo ananena pa tsiku limene maziko a nyumba ya Yehova wa makamu anayalidwa kuti kachisi amangidwe.+ 10 Masiku amenewo asanafike, anthu ndi ziweto sanali kulandira malipiro.+ Munthu wa pa ulendo, adani anali kumusowetsa mtendere,+ chifukwa ine ndinali kuyambanitsa anthu onse.’+

11 “‘Anthu anga otsala sindidzawachitiranso zinthu ngati zimene ndinawachitira masiku akale,’+ watero Yehova wa makamu. 12 ‘M’dzikolo mudzakhala mbewu ya mtendere.+ Mpesa udzabala zipatso+ ndipo dziko lapansi lidzapereka zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ake.+ Ndidzachititsa kuti anthu otsala+ mwa anthu awa adzalandire zinthu zonsezi.+ 13 Monga mmene munakhalira temberero pakati pa anthu a mitundu ina,+ inu a nyumba ya Yuda ndi a nyumba ya Isiraeli,+ ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala dalitso.+ Musachite mantha.+ Limbani mtima ndipo mukonzeke kugwira ntchito.’+

14 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘“Monga mmene ndinatsimikizira mtima kuchitapo kanthu pamene ndinakugwetserani tsoka chifukwa chakuti makolo anu anandikwiyitsa,+ ndipo sindinakumvereni chisoni,”+ watero Yehova wa makamu, 15 “tsopano ndatsimikizanso mtima kuchitapo kanthu, koma ulendo uno ndichitira zabwino Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda.+ Choncho musachite mantha.”’+

16 “‘Anthu inu muzichita zinthu izi:+ Muzilankhulana zoona zokhazokha.+ Poweruza milandu m’zipata za mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.+ 17 Musamakonzerane ziwembu mumtima mwanu kuti muonetsane tsoka+ ndipo musamakonde kulumbira monama.+ Pakuti zinthu zonsezi ine ndimadana nazo,’+ watero Yehova.”

18 Yehova wa makamu anapitiriza kundiuza kuti: 19 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Kusala kudya kwa m’mwezi wachinayi,+ kusala kudya kwa m’mwezi wachisanu,+ kusala kudya kwa m’mwezi wa 7+ ndiponso kusala kudya kwa m’mwezi wa 10,+ kudzakhala kusala kudya kosangalatsa ndi kokondweretsa kwa nyumba ya Yuda. Komanso nthawi za kusala kudya zimenezi zidzakhala nyengo zabwino zazikondwerero.+ Choncho muzikonda choonadi ndi kulimbikitsa mtendere.’+

20 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ndithu anthu a mitundu ina ndi anthu okhala m’mizinda yambiri adzabwera.+ 21 Anthu okhala mumzinda umodzi adzapita kwa anthu okhala mumzinda wina n’kuwauza kuti: “Tiyeni tipite!+ Tiyeni tipite kukakhazika pansi mtima+ wa Yehova ndi kufunafuna Yehova wa makamu. Inenso ndipita nawo.”+ 22 Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu ya anthu idzabweradi kudzafunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu.+ Idzabwera kudzakhazika pansi mtima wa Yehova.’

23 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’masiku amenewo, amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina+ adzagwira+ chovala cha munthu amene ndi Myuda+ ndi kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi,+ chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”’”+

9 Uthenga+ wokhudza dziko la Hadiraki:

“Awa ndi mawu a Yehova oweruza dziko la Hadiraki, ndipo akuweruzanso Damasiko.+ Pakuti maso a Yehova akuyang’ana anthu+ komanso mafuko onse a Isiraeli. 2 Mawu amenewa akuweruzanso Hamati+ amene anachita naye malire. Komanso akuweruza Turo+ ndi Sidoni+ chifukwa ali ndi nzeru zambiri.+ 3 Turo anamanga chiunda chomenyerapo nkhondo.* Anadziunjikira siliva wochuluka ngati dothi ndiponso golide wochuluka ngati matope a m’misewu.+ 4 Yehova adzamulanda chuma chake ndipo gulu lake lankhondo adzaliphera m’nyanja.+ Koma iye adzatenthedwa ndi moto.+ 5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha. Gaza adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitikiranso Ekironi+ chifukwa chakuti amene anali kumudalira+ adzachita manyazi. Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu ndipo m’dziko la Asikeloni simudzakhalanso anthu.+ 6 Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu+ adzakhala mu Asidodi,+ ndipo ine ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+ 7 Ndidzachotsa zinthu zake zamagazi m’kamwa mwake ndipo ndidzachotsa chakudya chake chonyansa pakati pa mano ake.+ Aliyense amene adzatsale adzakhala wa Mulungu wathu. Wotsalayo adzakhala ngati mfumu+ mu Yuda,+ ndipo Ekironi adzakhala ngati Myebusi.+ 8 Ndidzamanga msasa kunja kwa nyumba yanga kuti ndizidzailondera,+ moti sipadzakhalanso munthu wolowa kapena kutuluka. Kapitawo sadzadutsanso pakati pawo+ pakuti ine ndaona ndi maso anga zimene zinawachitikira.+

9 “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni sangalala kwambiri.+ Fuula mokondwera+ iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako+ ikubwera kwa iwe.+ Mfumuyo ndi yolungama ndipo yapambana.+ Iyo ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera nyama yokhwima, imene ndi mwana wamphongo wa bulu.+ 10 Ndidzawononga magaleta ankhondo mu Efuraimu ndiponso mahatchi mu Yerusalemu.+ Mauta omenyera nkhondo+ adzathyoledwa. Mfumuyo idzalankhula mawu amtendere kwa anthu a mitundu ina.+ Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja. Ndiponso udzachokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+

11 “Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,+ ndidzatulutsa akaidi ako+ m’dzenje lopanda madzi.

12 “Inu akaidi amene muli ndi chiyembekezo,+ bwererani kumalo a chitetezo champhamvu.+

“Komanso, ine lero ndikunena kuti, ‘Mkazi iwe, ndidzakupatsa magawo awiri a madalitso.+ 13 Yuda ndidzamupinda kuti akhale uta wanga. Efuraimu ndidzamuika pa uta umenewo ngati muvi. Iwe Ziyoni, ine ndidzadzutsa ana ako+ kuti aukire ana a Girisi.+ Ndipo ndidzakusandutsa lupanga la munthu wamphamvu.’+ 14 Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake,+ ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi.+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga lanyanga ya nkhosa,+ ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho ya kum’mwera.+ 15 Yehova wa makamu adzatchinjiriza anthu ake. Adani awo adzawalasa ndi miyala yoponya ndi gulaye* koma iwo adzagonjetsa adaniwo.+ Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.+ Adzadzazidwa ngati mbale zolowa ndiponso ngati mmene magazi amadzazira m’makona a guwa lansembe.+

16 “Pa tsiku limenelo, Yehova Mulungu adzapulumutsa nkhosa zake,+ zimene ndi anthu ake.+ Pakuti iwo adzakhala ngati miyala yonyezimira ya pachisoti chachifumu m’dziko lake.+ 17 Ubwino wake ndi waukulu kwambiri+ ndiponso iye ndi wooneka bwino kwambiri.+ Tirigu adzapatsa mphamvu anyamata ndipo vinyo watsopano adzapatsa mphamvu anamwali.”+

10 “Pemphani Yehova kuti akugwetsereni mvula+ pa nthawi ya mvula yomalizira.+ Pemphani Yehova amene anapanga mitambo yamvula+ ndiponso amene amagwetsera anthu mvula yamphamvu.+ Iye amapereka mbewu m’munda mwa munthu aliyense.+ 2 Aterafi*+ amalankhula zoipa. Ochita zamaula amaona masomphenya onama+ ndipo amafotokoza maloto opanda pake. Iwo saphula kanthu polimbikitsa anthu.+ N’chifukwa chake adzasochere ngati nkhosa.+ Iwo adzavutika chifukwa adzakhala opanda m’busa.+

3 “Mkwiyo wanga wayakira abusa,+ ndipo atsogoleri awo oipa ngati mbuzi+ ndiwaimba mlandu.+ Pakuti ine Yehova wa makamu ndacheukira gulu langa la nkhosa.+ Ndacheukira nyumba ya Yuda ndipo ndaisandutsa hatchi+ yanga yaulemerero, yokwera popita kunkhondo. 4 M’nyumba ya Yuda mudzatuluka mtsogoleri.+ Mudzatulukanso wolamulira ndi wothandiza,+ komanso mudzatuluka uta womenyera nkhondo.+ Kapitawo aliyense adzatuluka mwa iye.+ Anthu onsewa adzatuluka mwa iye. 5 Onsewa adzakhala ngati amuna amphamvu+ opondaponda matope a m’misewu ya kunkhondo.+ Iwo adzamenya nkhondo pakuti Yehova ali nawo.+ Adani awo oyenda pamahatchi adzachita manyazi.+ 6 Ndidzachititsa nyumba ya Yuda kukhala yapamwamba ndipo nyumba ya Yosefe ndidzaipulumutsa.+ Ndidzawachitira chifundo ndipo ndidzawapatsa malo okhala.+ Iwo adzakhala ngati sanakanidwepo chiyambire.+ Pakuti ine ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha.+ 7 A nyumba ya Efuraimu adzakhala ngati munthu wamphamvu+ ndipo adzasangalala mumtima mwawo ngati kuti amwa vinyo.+ Ana awo aamuna adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.+ Mitima yawo idzakondwera chifukwa cha Yehova.+

8 “‘Ndidzawaitana ndi likhweru+ ndi kuwasonkhanitsa pamodzi. Ndithu ine ndidzawawombola,+ ndipo iwo adzachuluka ngati anthu amene kale anali ambiri.+ 9 Ndidzawamwaza ngati mbewu pakati pa anthu a mitundu ina+ ndipo adzandikumbukira ali kumadera akutali.+ Iwowo ndi ana awo adzapezanso mphamvu ndipo adzabwerera.+ 10 Ndidzawabweretsa kuchokera kudziko la Iguputo.+ Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera ku Asuri.+ Ndidzawabweretsa kudera la Giliyadi+ ndi la Lebanoni chifukwa chakuti malo okwanira anthu onsewo sadzapezeka.+ 11 Ndidzadutsa panyanja, nyanjayo nditaigwetsera tsoka.+ Ndidzamenya mafunde a nyanjayo+ ndipo madzi onse a mtsinje wa Nailo adzauma.+ Kunyada kwa Asuri kudzathetsedwa+ ndipo ndodo yachifumu+ ya Iguputo idzachoka.+ 12 Ine Yehova ndidzawachititsa kukhala amphamvu+ ndipo zochita zawo zidzalemekeza dzina langa,’+ watero Yehova.”

11 “Iwe Lebanoni,+ tsegula zitseko zako kuti moto utenthe mitengo yako ya mkungudza.+ 2 Lira mofuula, iwe mtengo wofanana ndi mkungudza, chifukwa chakuti mtengo wa mkungudza wagwa, ndiponso mitengo ikuluikulu yawonongedwa.+ Lirani mofuula, inu mitengo ikuluikulu ya ku Basana, chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.+ 3 Tamverani! Abusa akulira mofuula+ chifukwa ulemerero wawo watha.+ Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula mofuula chifukwa nkhalango zowirira, za m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa.+

4 “Yehova Mulungu wanga wanena kuti, ‘Weta nkhosa zanga zimene zinayenera kuphedwa.+ 5 Amene anazigula anazipha+ koma sanaimbidwe mlandu.+ Amene akuzigulitsa+ akunena kuti: “Yehova atamandike pamene ine ndikupeza chuma.”+ Abusa ake sazichitira chifundo ngakhale pang’ono.’+

6 “‘Sindidzachitiranso chifundo anthu okhala m’dzikoli,’+ watero Yehova. ‘Choncho ine ndichititsa aliyense kuti aponderezedwe ndi mnzake+ ndiponso mfumu yake.+ Iwo adzawononga dzikoli, ndipo ine sindidzapulumutsa aliyense m’manja mwawo.’”+

7 Choncho ine ndinayamba kuweta nkhosa+ zimene zinayenera kuphedwa,+ ndipo ndinachita zimenezi chifukwa cha inu, anthu osautsika a m’gulu la nkhosali.+ Chotero ndinatenga ndodo ziwiri.+ Imodzi ndinaipatsa dzina lakuti Wosangalatsa.+ Inayo ndinaipatsa dzina lakuti Mgwirizano,+ ndipo ndinayamba kuweta gulu la nkhosalo. 8 Kenako ndinachotsa abusa atatu m’mwezi umodzi+ chifukwa sindinathenso kuleza nawo mtima,+ ndipo iwonso ananyansidwa nane. 9 Pambuyo pake ndinanena kuti: “Ndileka kukuwetani.+ Amene akufa, afe.+ Amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.”+ 10 Choncho ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Wosangalatsa+ ija ndi kuithyolathyola.+ Ndinachita izi kuti ndithetse pangano limene ndinapangana ndi anthu a mtundu wanga.+ 11 Panganolo linasweka pa tsiku limenelo. Mwa njira imeneyi, nkhosa zosautsika+ zimene zinali kundiona+ zinadziwa kuti zimene ndachitazo n’zimene Yehova ananena.

12 Kenako ndinawauza kuti: “Ngati mukuona kuti n’zoyenera,+ ndipatseni malipiro anga, koma ngati mukuona kuti n’zosayenera musandipatse.” Pamenepo iwo anandipatsa ndalama 30 zasiliva monga malipiro anga.+

13 Zitatero Yehova anandiuza kuti: “Kaziponye mosungiramo chuma.+ Zimenezi ndi ndalama za mtengo wapatali zimene akuona kuti angandigule nazo.”+ Choncho ndinatenga ndalama 30 zasilivazo n’kukaziponya mosungiramo chuma panyumba ya Yehova.+

14 Kenako ndinathyolathyola ndodo yanga yachiwiri ija yotchedwa Mgwirizano+ kuti ndithetse ubale+ wa Yuda ndi Isiraeli.+

15 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Tenga zida za m’busa wopanda pake.+ 16 Pakuti ndilola kuti m’dzikoli mukhale m’busa wina.+ M’busa ameneyu sadzasamala nkhosa zimene zikuwonongeka.+ Nkhosa yaing’ono sadzaifunafuna, ndipo yothyoka sadzaichiritsa.+ Nkhosa yotha kuima yokha sadzaipatsa chakudya, ndipo adzadya nyama ya nkhosa yonenepa.+ Iye adzakupula ziboda za nkhosazo.+ 17 Tsoka m’busa wanga wopanda pake+ amene akusiya nkhosa.+ Lupanga lidzamutema padzanja ndi kuboola diso lake la kudzanja lamanja. Dzanja lake lidzafota,+ ndipo diso lake la kudzanja lamanja lidzachita mdima.”

12 Uthenga wokhudza Isiraeli:

“Awa ndi mawu a Yehova okhudza Isiraeli.” Yehova, amene anatambasula miyamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi+ komanso kupanga mzimu+ n’kuuika mwa munthu, wanena kuti: 2 “Yerusalemu+ ndidzamusandutsa mbale yolowa yochititsa mitundu yonse ya anthu omuzungulira kuyenda dzandidzandi.+ Mdani adzazungulira Yuda, adzazungulira Yerusalemu.+ 3 Pa tsiku limenelo,+ Yerusalemu ndidzamusandutsa mwala wotopetsa+ kwa anthu a mitundu yonse. Onse onyamula mwala umenewo, ndithu adzatemekatemeka koopsa. Anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adzasonkhana pamodzi kuti amuukire.+ 4 Pa tsiku limenelo,+ ndidzachititsa hatchi+ iliyonse kudabwa kwambiri, ndipo wokwera pahatchiyo ndidzamuchititsa misala.+ Ndidzatsegula maso anga ndi kuyang’ana nyumba ya Yuda,+ ndipo hatchi iliyonse ya anthu a mitundu ina ndidzaichititsa khungu,” watero Yehova. 5 “Mafumu+ a Yuda adzanena mumtima mwawo kuti, ‘Anthu okhala mu Yerusalemu akutipatsa mphamvu zochokera kwa Mulungu wawo,+ Yehova wa makamu.’ 6 Pa tsiku limenelo, ndidzachititsa mafumu a Yuda kukhala ngati mbaula zamoto pakati pa mitengo,+ komanso ngati miyuni yamoto pamilu ya tirigu wongodula kumene.+ Iwo adzatentha mitundu yonse ya anthu owazungulira, mbali ya kudzanja lamanja ndi kudzanja lamanzere.+ Anthu a mu Yerusalemu adzakhalabe mumzinda wawo wa Yerusalemu.+

7 “Choyamba, Yehova adzapulumutsa mahema a Yuda. Choncho kukongola kwa nyumba ya Davide ndi kukongola kwa anthu okhala mu Yerusalemu, sikudzakhala kwakukulu kwambiri kuposa kwa Yuda. 8 Pa tsiku limenelo, Yehova adzatchinjiriza anthu okhala mu Yerusalemu.+ Munthu amene wapunthwa pa tsiku limenelo, adzakhala wamphamvu ngati Davide.+ Nyumba ya Davide idzawatsogolera ngati Mulungu,+ ndiponso ngati mngelo wa Yehova.+ 9 Pa tsiku limenelo, ndidzatsimikiza kuwononga mitundu yonse ya anthu imene ikubwera kudzaukira Yerusalemu.+

10 “Posonyeza kuti ndakomera mtima nyumba ya Davide ndi anthu okhala mu Yerusalemu, ndidzawapatsa mzimu wanga+ umene udzawalimbikitse kundipempha mochonderera.+ Ndithu iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa,+ ndipo adzamulirira ngati mmene amachitira polirira mwana yekhayo wamwamuna. Adzamulira mowawidwa mtima ngati mmene amachitira polira maliro a mwana wamwamuna woyamba kubadwa.+ 11 Pa tsiku limenelo, anthu adzalira kwambiri mu Yerusalemu ngati mmene analirira ku Hadadirimoni, m’chigwa cha Megido.+ 12 Anthu a m’dziko lonselo adzalira mokuwa.+ Banja lililonse lizidzalira palokha. Banja la nyumba ya Davide lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha.+ Banja la nyumba ya Natani+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha. 13 Banja la nyumba ya Levi+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha. Banja la Asimeyi+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’banja limeneli azidzalira paokha. 14 Mabanja onse otsala adzalira. Banja lililonse lizidzalira palokha, ndipo akazi a m’mabanjawo azidzalira paokha.+

13 “Pa tsiku limenelo,+ kudzakumbidwa chitsime+ kuti a m’nyumba ya Davide ndi anthu okhala mu Yerusalemu adzayeretsedwe ku machimo+ ndi ku zinthu zawo zonyansa.+

2 Yehova wa makamu wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathetsa mayina a mafano m’dziko lonseli+ ndipo mafanowo sadzakumbukiridwanso. M’dzikoli ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa.+ 3 Pakadzapezeka munthu aliyense wolosera, bambo ake ndi mayi ake amene anamubereka, adzamuuze kuti, ‘Iwe ufa ndithu, chifukwa walankhula zonama m’dzina la Yehova.’ Ndiyeno bambo ndi mayi akewo adzamulase chifukwa chakuti anali kulosera.+

4 “Zikadzatero, aneneri azidzachita manyazi pa tsiku limenelo.+ Azidzachita manyazi ndi masomphenya awo pamene akulosera. Sadzavalanso chovala chapadera chaubweya+ kuti anamize anthu. 5 Mneneri aliyense azidzanena kuti, ‘Ine si mneneri. Ndine mlimi, chifukwa munthu wina anandigula kuti ndikhale kapolo wake kuyambira ndili mnyamata.’ 6 Akadzafunsidwa kuti, ‘Kodi zilonda zimene zili pathupi pakozi watani?’ Iye azidzayankha kuti, ‘Zilonda zimenezi zinabwera chifukwa chomenyedwa m’nyumba ya anthu amene anali kundikonda kwambiri.’”

7 “Iwe lupanga, nyamuka ukanthe m’busa wanga.+ Ukanthe mwamuna wamphamvu yemwe ndi mnzanga,”+ watero Yehova wa makamu. “Ipha m’busa+ ndipo nkhosa zake zibalalike.+ Ine ndidzakomera mtima nkhosa zonyozeka.”+

8 “Ndiyeno magawo awiri mwa magawo atatu a anthu a m’dziko lonseli adzaphedwa.+ Koma gawo lachitatu la anthuwo lidzatsalamo,”+ watero Yehova. 9 “Ine ndidzatenga gawo lachitatulo n’kuliika pamoto+ kuti liyengeke. Ndidzawayenga ngati mmene amayengera siliva+ ndi kuwayeza ngati mmene amayezera golide.+ Gawo limeneli la anthu lidzaitana dzina langa, ndipo ine ndidzawayankha.+ Ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’+ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndi Mulungu wathu.’”+

14 “Tamverani! Tsiku la Yehova likubwera.+ Adani anu adzakulandani zinthu zanu n’kuzigawana ali mumzinda wanu womwewo. 2 Ndidzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu kuti imenyane ndi Yerusalemu.+ Mzindawu udzalandidwa,+ katundu wa m’nyumba adzatengedwa ndipo akazi adzagwiriridwa.+ Hafu ya anthu a mumzindawu idzatengedwa kupita kudziko lina,+ koma anthu otsala+ sadzachotsedwa mumzindawu.+

3 “Yehova adzapita kukamenyana ndi anthu a mitundu inawo+ ngati mmene anachitira pomenyana ndi adani ake m’mbuyomu.+ 4 Pa tsiku limenelo mapazi ake adzaponda paphiri la mitengo ya maolivi. Phiri limeneli lili moyang’anizana ndi Yerusalemu kumbali ya kum’mawa.+ Phiri la mitengo ya maolivi+ limeneli lidzagawanika pakati+ kuyambira kum’mawa mpaka kumadzulo. Zikadzatero, pakati pa mapiriwo padzakhala chigwa chachikulu kwambiri. Hafu imodzi ya phirilo idzasunthira kumpoto ndipo hafu inayo idzasunthira kum’mwera. 5 Anthu inu mudzathawira kuchigwa chimene chidzakhale pakati pa mapiri anga,+ chifukwa chakuti chigwacho chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa ngati mmene munachitira pothawa chivomezi chimene chinachitika m’masiku a Uziya, mfumu ya Yuda.+ Ndithu, Yehova Mulungu wanga adzabwera+ limodzi ndi oyera onse.+

6 “Pa tsiku limenelo, sipadzakhala kuwala kwapadera.+ Zinthu zidzaundana chifukwa cha kuzizira kwambiri.+ 7 Tsiku limenelo lidzatchedwa tsiku la Yehova.+ Sikudzakhala masana kapena usiku,+ chifukwa ngakhale usiku kudzakhala kukuwalabe.+ 8 Pa tsiku limenelo madzi amoyo+ adzatuluka mu Yerusalemu.+ Hafu ya madziwo idzapita kunyanja ya kum’mawa+ ndipo hafu inayo idzapita kunyanja ya kumadzulo.+ Zimenezi zidzachitika m’chilimwe ndiponso m’nyengo yozizira.+ 9 Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse lapansi.+ Pa tsiku limenelo, Yehova adzakhala mmodzi+ ndipo dzina lake lidzakhala limodzi.+

10 “Dziko lonse lidzasintha ndi kukhala ngati chigwa cha Araba+ kuyambira ku Geba+ kukafika ku Rimoni+ kum’mwera kwa Yerusalemu. Mzindawu udzakwezedwa pamalo ake ndipo anthu adzakhalamo.+ Anthuwo adzakhalamo kuyambira ku Chipata cha Benjamini+ mpaka ku Chipata Choyamba, kukafika ku Chipata cha Pakona. Komanso adzakhala kuyambira ku Nsanja ya Hananeli+ mpaka kukafika kumalo a mfumu oponderamo mphesa. 11 Anthu adzakhala mumzindawo ndipo simudzakhalanso zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Anthu okhala mu Yerusalemu, adzakhala mmenemo ali otetezeka.+

12 “Mliri umene Yehova adzagwetsere anthu onse a mitundu ina amene adzamenyane ndi Yerusalemu ndi uwu:+ Munthu aliyense mnofu wake udzawola ali chiimire,+ maso ake adzawola ali m’malo mwake ndiponso lilime lake lidzawola m’kamwa mwake.

13 “Pa tsiku limenelo Yehova adzawasokoneza kwambiri.+ Aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo aliyense adzamenya mnzake ndi dzanja lake. 14 Yuda nayenso adzamenya nkhondo mothandizana ndi Yerusalemu, ndipo adzasonkhanitsa chuma cha anthu a mitundu yonse yowazungulira. Adzasonkhanitsa golide, siliva ndi zovala zambirimbiri.+

15 “Mliri wofanana ndi umenewu udzagweranso mahatchi, nyulu,* ngamila, abulu amphongo ndi chiweto cha mtundu uliwonse chimene chidzapezeke m’misasa ya adaniwo.

16 “Aliyense wotsala mwa anthu a mitundu yonse amene akubwera kudzamenyana ndi Yerusalemu,+ azidzapita kukagwadira Mfumu,+ Yehova wa makamu,+ chaka ndi chaka,+ ndi kukachita nawo chikondwerero cha misasa.+ 17 Aliyense wochokera m’mabanja+ a padziko lapansi, amene sadzapita+ ku Yerusalemu kukagwadira Mfumu, Yehova wa makamu, mvula sidzagwa m’dziko lake.+ 18 Ngati banja la Iguputo silidzabwera mumzindawu, m’dziko lawonso simudzagwa mvula. Mliri umene Yehova adzagwetsere mitundu ina ya anthu amene sazidzabwera kudzachita chikondwerero cha misasa, udzawagwera. 19 Chimenechi chidzakhala chilango cha Iguputo chifukwa cha tchimo lake komanso chifukwa cha tchimo la anthu onse a mitundu ina amene sazidzabwera kudzachita nawo chikondwerero cha misasa.+

20 “Pa tsiku limenelo, pamabelu a mahatchi padzalembedwa mawu+ akuti ‘Chiyero n’cha Yehova!’+ Ndipo miphika yakukamwa kwakukulu+ ya m’nyumba ya Yehova adzaigwiritsa ntchito ngati mbale zolowa+ za paguwa lansembe.+ 21 Mphika uliwonse wakukamwa kwakukulu mu Yerusalemu ndi mu Yuda udzakhala woyera ndipo udzakhala wa Yehova wa makamu. Anthu onse amene azidzapereka nsembe azidzabwera n’kutengako ina mwa miphikayo ndi kuphikiramo.+ Pa tsiku limenelo, m’nyumba ya Yehova wa makamu+ simudzapezeka Mkanani.”+

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.

Mawu ake enieni, “ngati mphepo zinayi zam’mlengalenga.”

“Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

“Muyezo wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.

Mawu ake enieni, “ndilire.”

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 31:19.

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena