YONA
1 Yehova analankhula ndi Yona*+ mwana wa Amitai, kuti: 2 “Nyamuka upite kumzinda waukulu wa Nineve.+ Kumeneko ukalengeze uthenga wachiweruzo kwa anthu amumzindawo chifukwa ndaona zoipa zimene akuchita.”
3 Koma Yona ananyamuka nʼkulowera ku Tarisi, kuthawa Yehova. Atafika ku Yopa anapeza chombo chopita ku Tarisi. Iye analipira ndalama za ulendowo pothawa Yehova nʼkukwera chombocho kuti apite ku Tarisi limodzi ndi anthu amene anali mmenemo.
4 Ndiyeno Yehova anabweretsa mphepo yamphamvu panyanja, ndipo kenako panachitika chimkuntho choopsa, moti chombocho chinatsala pangʼono kusweka. 5 Oyendetsa chombo anachita mantha kwambiri ndipo aliyense anayamba kuitana mulungu wake kuti amuthandize. Iwo anayamba kuponya mʼnyanja katundu amene anali mʼchombocho kuti chipepukidwe.+ Apa nʼkuti Yona atatsikira mkatikati mwa chombocho nʼkugona tulo tofa nato. 6 Kenako woyendetsa chombo anapita pamene Yona anagona nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukungogona? Tadzuka uitane mulungu wako! Mwina Mulungu woona atikomera mtima ndipo sitifa.”+
7 Ndiyeno anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tichite maere+ kuti tidziwe amene wachititsa kuti tsokali litigwere.” Choncho anachitadi maere ndipo maerewo anagwera Yona.+ 8 Ndiyeno anamufunsa kuti: “Tiuze, ndani wachititsa kuti tsoka limeneli litigwere? Umagwira ntchito yanji ndipo ukuchokera kuti? Kwanu nʼkuti ndipo ndiwe wa mtundu uti?”
9 Iye anayankha kuti: “Ndine Mheberi ndipo ndimaopa* Yehova Mulungu wakumwamba, amene anapanga nyanja ndi mtunda.”
10 Anthuwo atamva zimenezi anachita mantha kwambiri, ndipo anamufunsa kuti: “Wachitiranji zimenezi?” (Anthuwo anadziwa kuti Yona akuthawa Yehova, chifukwa iye anali atawauza zimenezo.) 11 Kenako anamufunsa kuti: “Ndiye tichite nawe chiyani kuti nyanjayi ikhale bata?” Apa nʼkuti chimkuntho choopsa chija chikukulirakulira. 12 Iye anawayankha kuti: “Mundinyamule nʼkundiponya mʼnyanjamu ndipo nyanjayi ikhala bata. Ndikudziwa kuti mkunthowu ukuchitika chifukwa cha ine.” 13 Koma anthuwo anayesetsa kuti adutse mafunde amphamvuwo nʼkukafika kumtunda. Komabe sanakwanitse chifukwa mkunthowo unkawonjezeka kwambiri.
14 Kenako anthuwo anafuulira Yehova kuti: “Chonde Yehova, musalole kuti tife chifukwa cha munthu uyu! Musatiimbe mlandu wa magazi a munthu wosalakwa, chifukwa inu Yehova mwachita zimene mumafuna.” 15 Kenako ananyamula Yona nʼkumuponya mʼnyanja ndipo nyanjayo inakhala bata. 16 Zitatero anthuwo anaopa kwambiri Yehova.+ Choncho anapereka nsembe kwa Yehova ndipo analonjeza kuti azimutumikira.
17 Tsopano Yehova anatumiza chinsomba chachikulu kuti chikameze Yona moti Yona anakhala mʼmimba mwa nsomba masiku atatu, masana ndi usiku.+
2 Kenako Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake, ali mʼmimba mwa chinsombacho.+ 2 Iye anati:
“Nditavutika kwambiri ndinaitana inu Yehova ndipo munandiyankha.+
Ndinafuula kupempha thandizo ndili mʼManda* akuya,+
Ndipo inu munamva mawu anga.
Mafunde anu amphamvu anadutsa pamwamba panga.+
4 Ndipo ine ndinati, ‘Mwandithamangitsa pamaso panu!
Kodi kachisi wanu woyera ndidzamuonanso?’
Zomera zamʼnyanja zinakulunga mutu wanga.
6 Ndinamira mpaka mʼmunsi mwenimweni mwa mapiri.
Zotsekera za dziko lapansi zinayamba kunditsekereza kuti ndikhale komweko mpaka kalekale.
Koma inu Yehova Mulungu wanga, munanditulutsa mʼdzenje ndili wamoyo.+
7 Nditatsala pangʼono kufa, ndinakumbukira Yehova.+
Ndipo pemphero langa linafika kwa inu mʼkachisi wanu woyera.+
8 Anthu okhulupirira mafano opanda pake, amasiya Mulungu amene angawasonyeze chikondi chokhulupirika.*
9 Koma ine, ndidzakutamandani ndi kupereka nsembe kwa inu.
Zimene ndalonjeza ndidzazikwaniritsa.+
Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”+
10 Kenako Yehova analamula chinsomba chija ndipo chinalavula Yona kumtunda.
3 Yehova analankhula ndi Yona kachiwiri kuti:+ 2 “Nyamuka, upite kumzinda waukulu wa Nineve,+ ndipo ukalalikire uthenga umene ndikuuze.”
3 Choncho Yona ananyamuka nʼkupita ku Nineve+ pomvera mawu a Yehova.+ Mzinda wa Nineve unali waukulu kwambiri* ndipo mtunda wake unali woyenda masiku atatu. 4 Kenako Yona analowa mumzindawo nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.”
5 Anthu a ku Nineve anakhulupirira Mulungu+ ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli. 6 Uthengawo utafika kwa mfumu ya Nineve, mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu nʼkuvula chovala chake chachifumu. Kenako inavala chiguduli nʼkukhala paphulusa. 7 Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamula anthu kuti alengeze mu Nineve kuti:
“Mfumu ndi akuluakulu ake alamula kuti: Munthu aliyense, ngʼombe, nkhosa komanso chiweto chilichonse zisadye chilichonse. Munthu aliyense kapena chiweto zisadye chakudya kapena kumwa madzi. 8 Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo aliyense asiye zinthu zoipa komanso zachiwawa zimene amachita. 9 Ndani angadziwe, mwina Mulungu woona asintha maganizo pa zimene amafuna kuchita ndipo abweza mkwiyo wake woyaka moto, moti satiwononga?”
10 Mulungu woona ataona zimene anachita, kuti anasiya kuchita zoipa,+ anasintha maganizo ake ndipo sanawabweretsere tsoka limene ananena kuti awabweretsera.+
4 Koma zimenezi sizinamusangalatse Yona ngakhale pangʼono moti anakwiya koopsa. 2 Choncho iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Inu Yehova, kodi zimene ndimaopa ndili kwathu zija si zimenezi? Nʼchifukwa chaketu ndinkafuna kuthawira ku Tarisi.+ Ndinadziwa kuti inu ndinu Mulungu wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka+ komanso mumamva chisoni mukafuna kubweretsa tsoka. 3 Inu Yehova, chotsani moyo wanga, chifukwa kuli bwino ndingofa kusiyana nʼkuti ndikhale ndi moyo.”+
4 Yehova anamufunsa kuti: “Kodi pali chifukwa choti ukwiyire choncho?”
5 Kenako Yona anatuluka mumzindawo nʼkukakhala pansi kumʼmawa kwa mzindawo. Kumeneko anamanga kachisakasa kuti akhale pamthunzi podikira kuti aone zimene zichitikire mzindawo.+ 6 Ndiyeno Yehova Mulungu anameretsa chomera cha mtundu wa mphonda* kuti chiyange pamene Yona anakhala. Anachita zimenezi kuti pakhale mthunzi nʼcholinga choti apeze mpumulo. Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha chomeracho.
7 Koma Mulungu woona anatumiza mbozi mʼbandakucha wa tsiku lotsatira kuti ikadye chomera cha mtundu wa mphondacho, moti chinafota. 8 Dzuwa litatuluka, Mulungu anatumizanso mphepo yotentha yochokera kumʼmawa. Dzuwa linawotcha kwambiri Yona moti anangotsala pangʼono kukomoka. Choncho Yona anapempha mobwerezabwereza kuti angofa. Iye ankanena kuti: “Kuli bwino ndingofa kusiyana nʼkuti ndikhale ndi moyo.”+
9 Ndiyeno Mulungu anafunsa Yona kuti: “Kodi pali chifukwa choti ukwiyire ndi chomera cha mtundu wa mphondachi?”+
Yona anayankha kuti: “Ndikuyeneradi kukwiya, ndakwiya kwambiri moti ndikufuna kufa.” 10 Koma Yehova anati: “Iwe ukumvera chisoni chomera cha mtundu wa mphondachi, chimene sunachivutikire kapena kuchikulitsa, chimene changomera usiku umodzi wokha kenako nʼkufa. 11 Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve,+ mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika?* Kodi sindiyenera kumveranso chisoni ziweto zawo zambiri?”+
Kutanthauza “Nkhunda.”
Kapena kuti, “ndimalambira.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “amasiya kukhulupirika kwawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mulungu ankauona kuti ndi mzinda waukulu.”
Mabaibulo ena amati, “nsatsi.”
Kapena kuti, “dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.”