Maliro
א [ʼAʹleph]
1 Amene anali ndi anthu ambiri+ tsopano wakhala wopanda anthu.+
Amene anali ndi anthu ambiri pakati pa mitundu ina+ wakhala ngati mkazi wamasiye.+
Amene anali wolemekezeka pakati pa zigawo zina wayamba kugwira ntchito yaukapolo.+
ב [Behth]
2 Iye akulira kwambiri usiku,+ ndipo misozi ikutsika pamasaya ake.+
Pakati pa onse amene anali kumukonda, palibe amene akumutonthoza.+
Anthu onse amene anali anzake amuchitira zachinyengo+ ndipo akhala adani ake.+
ג [Giʹmel]
3 Yuda wakhala kapolo chifukwa cha nsautso+ ndiponso chifukwa cha kukula kwa ntchito yaukapolo imene akugwira.+
Iye wakhala pakati pa mitundu ina ya anthu,+ ndipo sanapeze malo ampumulo.
Onse amene anali kumuzunza amupeza pa nthawi ya mavuto ake.+
ד [Daʹleth]
4 Njira zopita ku Ziyoni zikulira, chifukwa palibe amene akupita kuchikondwerero.+
Zipata zake zonse zasiyidwa.+ Ansembe+ ake akuusa moyo.*
Anamwali ake agwidwa ndi chisoni,+ ndipo iyeyo akumva kuwawa mumtima.
ה [Heʼ]
5 Adani ake akumulamulira.+ Anthu odana naye sakuda nkhawa.+
Yehova wamuchititsa kukhala wachisoni chifukwa cha kuchuluka kwa machimo+ ake,
Ndipo ana ake ayenda patsogolo pa adani awo atagwidwa ukapolo.+
ו [Waw]
6 Ulemerero+ wonse wamuchokera mwana wamkazi wa Ziyoni.
Akalonga ake akhala ngati mbawala zamphongo zimene zikusowa msipu.+
ז [Zaʹyin]
7 Yerusalemu anakumbukira zinthu zake zonse zabwino+ zimene anali nazo kuyambira kalekale.
Anazikumbukira m’masiku a masautso ake ndi a anthu ake osowa pokhala.
Anthu ake atagwidwa ndi adani, pamene iye analibe munthu womuthandiza,+
Adani akewo anamuona, ndipo anamuseka+ chifukwa chakuti wagwa.
ח [Chehth]
8 Yerusalemu wachita tchimo+ lalikulu. N’chifukwa chake wakhala chinthu chonyansa.+
Onse amene anali kumulemekeza ayamba kumuona ngati chinthu chachabechabe,+ chifukwa aona maliseche+ ake.
Iyenso akuusa moyo+ ndipo watembenukira kwina chifukwa cha manyazi.
ט [Tehth]
9 Zovala+ zake ndi zodetsedwa. Iye sanaganizire za tsogolo+ lake.
Wagwa modabwitsa ndipo alibe womutonthoza.+
Inu Yehova, onani kusautsika+ kwanga, pakuti mdani wanga akudzitukumula.+
י [Yohdh]
10 Mdani watambasula dzanja lake n’kutenga zinthu+ zake zonse zabwino.
Yerusalemu waona mitundu ina itabwera ndi kulowa m’malo ake opatulika,+
Mitundu imene munalamula kuti isalowe mumpingo wanu.
כ [Kaph]
11 Anthu ake onse akuusa moyo. Iwo akufunafuna chakudya.+
Asinthanitsa zinthu zawo zabwino ndi chakudya kuti adzitsitsimutse.+
Inu Yehova ndiyang’aneni. Onani kuti ndakhala ngati mkazi wachabechabe.+
ל [Laʹmedh]
12 Inu nonse amene mukudutsa m’njira, kodi mukuona ngati imeneyi ndi nkhani yaing’ono? Ndiyang’aneni kuti muone.+
Kodi palinso ululu wina woposa ululu umene ineyo ndalangidwa nawo,+
Ululu umene Yehova wandibweretsera nawo chisoni m’tsiku la mkwiyo+ wake woyaka moto?
מ [Mem]
13 Iye watumiza moto m’mafupa+ mwanga kuchokera kumwamba, ndipo wafooketsa fupa lililonse.
Watchera ukonde+ kuti ukole mapazi anga. Wandibweza kumbuyo.
Wandisandutsa mkazi wosiyidwa popanda thandizo. Ndikudwala tsiku lonse.+
נ [Nun]
14 Iye wakhala tcheru kuti aone machimo+ anga. Machimowo alukanalukana m’dzanja lake.
Amangidwa m’khosi+ mwanga, moti mphamvu zanga zatha.
Yehova wandipereka m’manja mwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo.+
ס [Saʹmekh]
15 Yehova wandichotsera anthu anga onse amphamvu+ ndi kuwakankhira pambali.
Wandiitanitsira msonkhano kuti athyolethyole anyamata anga.+
Yehova wapondaponda moponderamo mphesa+ mwa namwali, mwana wamkazi wa Yuda.+
ע [ʽAʹyin]
16 Ndikulirira zinthu zimenezi ngati mkazi.+ Maso anga ine! Maso anga akutuluka misozi.+
Pakuti wonditonthoza, munthu woti anditsitsimule, ali kutali ndi ine.
Ana anga asiyidwa+ popanda thandizo, pakuti mdani wanga wadzitukumula.+
פ [Peʼ]
17 Ziyoni watambasula manja ake.+ Iye alibe womutonthoza.+
Yehova walamula onse ozungulira Yakobo kuti akhale adani ake.+
Yerusalemu wakhala chinthu chonyansa pakati pawo.+
צ [Tsa·dhehʹ]
18 Yehova ndi wolungama,+ koma ine ndapandukira+ mawu a pakamwa pake.
Anthu nonsenu, tamverani mawu anga, ndipo muone ululu umene ndikumva.
Anamwali anga ndi anyamata anga atengedwa kupita ku ukapolo.+
ק [Qohph]
19 Ndaitana anthu ondikonda kwambiri,+ koma anthuwo andichitira zachinyengo.
Ansembe anga ndiponso akuluakulu atha+ mumzinda.
Atha pamene anali kufunafuna chakudya choti adye kuti adzitsitsimutse.+
ר [Rehsh]
20 Taonani, inu Yehova. Inetu zandivuta. M’mimba mwanga mukubwadamuka.+
ש [Shin]
21 Anthu amva mmene ndikuusira moyo ngati mkazi,+ koma palibe wonditonthoza.+
Adani anga onse amva za tsoka+ langa. Iwo akondwera,+ chifukwa ndinu mwachititsa zimenezi.
Inu mubweretsadi tsiku limene mwanena,+ kuti iwo akhale ngati ine.+
ת [Taw]