2 Samueli
kapena, malinga ndi Baibulo lachigiriki la Septuagint, MAFUMU WACHIWIRI
1 Sauli atamwalira, ndiponso Davide atabwera kuchokera kokakantha Aamaleki,+ Davideyo anakhala ku Zikilaga+ masiku awiri. 2 Ndiyeno pa tsiku lachitatu anaona munthu wina+ akubwera kuchokera kumsasa, kwa Sauli. Iye anali atang’amba zovala zake+ komanso atadzithira dothi kumutu.+ Atafika kwa Davide, nthawi yomweyo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ kenako anagona pansi.
3 Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Wachokera kuti?” Poyankha iye anati: “Ndathawa kumsasa wa Isiraeli.” 4 Kenako Davide anamufunsa kuti: “Zayenda bwanji kumeneko? Chonde, ndiuze.” Iye anayankha kuti: “Anthu athawa kunkhondo komanso anthu ambiri agwa ndipo afa,+ ngakhalenso Sauli+ ndi mwana wake Yonatani+ afa.” 5 Pamenepo Davide anafunsa mnyamata amene anali kumuuza nkhaniyo kuti: “Iweyo wadziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afadi?”+ 6 Mnyamatayo anayankha kuti: “Ndinapezeka kuti ndili paphiri la Giliboa,+ ndipo ndinaona Sauli atatsamira mkondo+ wake. Zili choncho, ndinaona asilikali oyenda m’magaleta ndi asilikali okwera pamahatchi* akumuyandikira.+ 7 Sauliyo atatembenuka n’kundiona, anandiitana, ndipo ine ndinayankha kuti, ‘Ine mbuyanga!’ 8 Kenako anandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe ndani?’ Ine ndinamuyankha kuti, ‘Ndine Mwamaleki.’+ 9 Ndiyeno anandiuza kuti, ‘Bwera kuno chonde, undiphe pakuti zinthu zandivuta,* koma ndidakali ndi moyo.’+ 10 Choncho ndinapita pamene iye anali ndi kumupha,+ chifukwa ndinadziwa kuti sakhalanso ndi moyo popeza anali atavulala kwambiri. Kenako ndinatenga chisoti chachifumu+ chimene anavala ndi khoza limene linali kudzanja lake kuti ndibwere nazo kuno kwa inu mbuyanga.”
11 Davide atamva zimenezi anagwira zovala zake ndi kuzing’amba.+ Nawonso amuna onse amene anali ndi Davide anang’amba zovala zawo. 12 Atatero, anayamba kulira ndi kubuma+ komanso kusala kudya+ mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi Yonatani mwana wake, komanso chifukwa cha anthu a Yehova ndi anthu a nyumba ya Isiraeli,+ amene anali atakanthidwa ndi lupanga.
13 Ndiyeno Davide anafunsa mnyamata amene anali kumuuza nkhaniyo kuti: “Kodi kwanu n’kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndine mwana wa Mwamaleki, mlendo wokhala pakati pa Aisiraeli.”+ 14 Pamenepo Davide anati: “Zinatheka bwanji iwe osaopa+ kutambasula dzanja lako ndi kukantha wodzozedwa+ wa Yehova?” 15 Atatero, Davide anaitana mmodzi mwa anyamata ake ndi kumuuza kuti: “Mukanthe.” Chotero anamukanthadi, moti anafa.+ 16 Kenako Davide anamuuza kuti: “Mlandu wa magazi ako ukhale pamutu pako,+ chifukwa wadzichitira wekha umboni+ ponena kuti, ‘Ineyo ndapha wodzozedwa wa Yehova.’”+
17 Ndiyeno Davide anayamba kuimba nyimbo iyi yoimba polira,+ pamene anali kulira Sauli ndi Yonatani mwana wake.+ 18 Iye ananenanso kuti, ana a Yuda+ aphunzitsidwe nyimboyi, yotchedwa “Uta.”+ Nyimbo imeneyi inalembedwa m’buku la Yasari:+
19 “Isiraeli iwe, anthu ako aulemerero aphedwa pamalo ako okwezeka.+
Haa! Anthu amphamvu agwa.
20 Anthu inu musanene zimenezi mumzinda wa Gati.+
Musalengeze zimenezi m’misewu ya Asikeloni,+
Kuopera kuti ana aakazi a Afilisiti angasangalale,+
Kuopera kuti ana aakazi a anthu osadulidwa angakondwere.
21 Inu mapiri a Giliboa,+ musalole kuti mame kapena mvula igwe pa inu. Musalole kuti minda imene ili pa inu ibale zipatso zokaperekedwa kwa Mulungu.*+
Chifukwa pa inu chishango cha amuna amphamvu chinadetsedwa,
Chishango cha Sauli, moti palibenso chishango chimene chinadzozedwa ndi mafuta.+
22 Uta wa Yonatani sunkalephera kupha adani ndi kukhetsa magazi awo,
Sunkalephera kubaya mafuta a anthu amphamvu.+
Lupanga la Sauli silinkabwerako chabe osakwaniritsa ntchito yake.+
23 Sauli ndi Yonatani,+ anthu okondeka ndi osangalatsa pamene anali ndi moyo,
Ngakhale pa imfa yawo sanasiyane.+
Iwo anali aliwiro kuposa chiwombankhanga,+
Amphamvu kuposa mikango.+
24 Ana aakazi a Isiraeli inu, mulirireni Sauli,
Amene anakuvekani zovala zamtengo wapatali* ndi zinthu zokongoletsa,
Amene anaika zokongoletsa zagolide pazovala zanu.+