Miyambo
2 Mwana wanga, ukamvera mawu anga+ ndi kusunga malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali,+ 2 ukamvetsera nzeru ndi khutu lako,+ ukaika mtima wako pa kuzindikira,+ 3 komanso ukaitana kumvetsa zinthu+ ndi kufuulira kuzindikira,+ 4 ukamazifunafuna ngati siliva,+ ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+ 5 udzamvetsa tanthauzo la kuopa+ Yehova ndipo udzamudziwadi Mulungu.+ 6 Pakuti Yehova amapereka nzeru.+ Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake.+ 7 Anthu owongoka mtima, iye amawasungira nzeru zopindulitsa.+ Kwa anthu oyenda ndi mtima wosagawanika, iye amakhala chishango+ 8 mwa kuyang’anitsitsa njira zachiweruzo,+ ndipo adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.+ 9 Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.+
10 Nzeru zikalowa mumtima mwako,+ ndipo kudziwa zinthu kukakhala kosangalatsa m’moyo wako,+ 11 kuganiza bwino kudzakuyang’anira,+ ndipo kuzindikira kudzakuteteza,+ 12 kuti kukupulumutse kunjira yoipa,+ ndiponso kwa munthu wonena zinthu zopotoka,+ 13 komanso kwa anthu amene amasiya njira zowongoka kuti ayende m’njira za mdima.+ 14 Kudzakupulumutsanso kwa anthu amene amasangalala kuchita zoipa,+ amene amakondwera ndi zinthu zoipa ndi zopotoka,+ 15 amene njira zawo ndi zokhota ndiponso amene ali achinyengo m’zochita zawo zonse.+ 16 Kudzakupulumutsa kwa mkazi wachilendo, mkazi wochokera kwina+ wolankhula mwaukathyali,+ 17 amene wasiya mnzake wapamtima wa pachitsikana chake+ ndiponso amene waiwala pangano limene anapangana ndi Mulungu wake.+ 18 Pakuti nyumba yake imatsikira kumanda ndipo njira zake zimatsikira kwa akufa.+ 19 Onse ogona naye sadzabwerera ndipo iwo sadzapezanso njira za amoyo.+
20 Cholinga cha zonsezi n’chakuti uziyenda m’njira ya anthu abwino+ ndi kuti uzisunga njira za anthu olungama.+ 21 Pakuti owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi,+ ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo.+ 22 Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi+ ndipo achinyengo adzazulidwamo.+