Ezekieli
22 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, kodi ndiwe wokonzeka kuweruza?+ Kodi uweruza mzinda umene uli ndi mlandu wa magaziwu+ ndi kuudziwitsa zonyansa zake zonse?+ 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mzinda umene ukukhetsa magazi+ kufikira nthawi yako yoweruzidwa itakwana,+ iwe mzinda umene wapanga mafano onyansa kuti udzidetse nawo,+ 4 uli ndi mlandu wa magazi amene wakhetsa+ ndipo wadzidetsa chifukwa cha mafano onyansa amene wapanga.+ Wafupikitsa masiku a moyo wako ndipo zaka zoti ulandire chilango zafika. Choncho ndidzakusandutsa chinthu chotonzedwa pakati pa mitundu ina ya anthu ndiponso ndidzakusandutsa chinthu chimene mayiko onse adzachiseka ndi kuchikuwiza.+ 5 Mayiko amene uli nawo pafupi ndiponso amene ali kutali ndi iwe adzakukuwiza, iwe mzinda wa dzina lodetsedwa komanso wachisokonezo chachikulu.+ 6 Mwa iwetu muli atsogoleri+ a Isiraeli. Aliyense wa iwo akugwiritsa ntchito dzanja lake modzipereka kuti akhetse magazi.+ 7 Anthu anyoza abambo ndi amayi awo mwa iwe.+ Mlendo wokhala mwa iwe amuchitira zinthu mwachinyengo.+ Azunza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.”’”+
8 “‘Iwe wanyoza malo anga oyera, ndipo wadetsa sabata langa.+ 9 Mwa iwe muli anthu amiseche amene akukhetsa magazi.+ Iwo amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri.+ Achita khalidwe lotayirira mwa iwe.+ 10 Anthu avula bambo awo.+ Iwo agona ndi mkazi wodetsedwa amene akusamba.+ 11 Munthu wachita zinthu zonyansa ndi mkazi wa mnzake,+ ndipo munthu wachita khalidwe lotayirira mwa kugona ndi mkazi wa mwana wake.+ Munthu wagona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake.+ 12 Anthu alandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe walandira chiwongoladzanja+ ndi kuchita katapira.+ Ukupeza phindu losayenera mwa kubera anzako+ mwachinyengo+ ndipo ine wandiiwala,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
13 “‘Ine ndawomba m’manja*+ chifukwa cha phindu lachinyengo limene wapeza+ komanso chifukwa cha zochita zako zokhetsa magazi zimene zili pakati pako.+ 14 Kodi mtima wako udzapitiriza kupirira,+ kapena kodi manja ako adzakhala ndi mphamvu m’masiku amene ndidzakulange?+ Ine Yehova ndanena ndipo ndidzachitapo kanthu.+ 15 Anthu ako ndidzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndipo ndidzawamwaza m’mayiko osiyanasiyana.+ Komanso ndidzachotsa zodetsa zako mwa iwe.+ 16 Ndithudi udzaipitsidwa pamaso pa mitundu ina, ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+
17 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kwa ine a nyumba ya Isiraeli akhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo.+ Onsewo ali ngati mkuwa, tini, chitsulo ndi mtovu m’ng’anjo. Iwo akhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga siliva.+
19 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti nonsenu mwakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo,+ ine ndikusonkhanitsani pamodzi mu Yerusalemu.+ 20 Ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu amenewa ndili wokwiya ndiponso waukali. Ndidzawasonkhanitsa ngati mmene anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo,+ mtovu ndi tini m’ng’anjo kuti zinthu zimenezi azikolezere+ moto ndi kuzisungunula.+ Choncho anthu inu ndidzakukolezerani moto ndi kukusungunulani. 21 Ndidzakusonkhanitsani pamodzi ndi kukukolezerani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo mudzasungunuka mumzindawo.+ 22 Monga mmene anthu amasungunulira siliva m’ng’anjo, inenso ndidzakusungunulani mumzindawo. Chotero inu mudzadziwa kuti ine Yehova ndakutsanulirani mkwiyo wanga.’”+
23 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, uza dzikoli kuti, ‘Iwe ndiwe dziko limene silikuyeretsedwa. Pa tsiku limene udzadzudzulidwe mwamphamvu, mwa iwe simudzagwa mvula.+ 25 Aneneri ako akukonza chiwembu mwa iwe.+ Iwo akukhadzula anthu+ ngati mkango wobangula umene wagwira nyama.+ Akulanda anthu chuma ndi zinthu zawo zamtengo wapatali.+ Achulukitsa akazi amasiye mmenemo.+ 26 Ansembe ako aphwanya chilamulo changa modzionetsera,+ ndipo akuipitsa malo anga oyera.+ Sakusiyanitsa+ zinthu zoyera ndi zinthu wamba.+ Sanauze anthu kusiyana kwa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyera.+ Anyalanyaza sabata langa+ ndipo andichitira mwano pakati pawo.+ 27 Atsogoleri a mumzindawo ali ngati mimbulu yomwe ikukhadzula nyama. Iwo akukhetsa magazi+ ndiponso kuwononga miyoyo n’cholinga chopeza phindu mwachinyengo.+ 28 Aneneri a mumzindawo apaka laimu machimo a atsogoleriwo.+ Aona masomphenya onama+ ndipo akuloserera atsogoleriwo zinthu zabodza.+ Iwo akunena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,” pamene Yehova sananene chilichonse. 29 Anthu a m’dzikolo abera anthu pochita zachinyengo+ ndiponso zauchifwamba.+ Iwo akuzunza anthu osautsika ndi osauka.+ Abera mlendo pochita zachinyengo komanso zopanda chilungamo.’+
30 “‘Ndinafunafuna munthu pakati pawo amene angathe kukonzanso mpanda wamiyala+ ndi kuima pamalo ogumuka a mpandawo+ kuti ateteze dzikolo n’cholinga choti ine ndisaliwononge,+ koma sindinapeze aliyense. 31 Choncho ndidzawadzudzula mwamphamvu.+ Ndidzawafafaniza ndi moto wa mkwiyo wanga.+ Ndidzawalanga malinga ndi zochita zawo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”