Yesaya
19 Uwu ndi uthenga wokhudza Iguputo:+ Taonani! Yehova wakwera mtambo wothamanga+ ndipo akubwera mu Iguputo. Milungu yopanda pake ya ku Iguputo idzanjenjemera chifukwa chomuopa+ ndipo mitima ya Aiguputo idzasungunuka mkati mwa dzikolo.+
2 “Ndidzachititsa kuti Aiguputo ayambane ndi Aiguputo anzawo. Aliyense adzamenyana ndi m’bale wake ndipo aliyense adzamenyana ndi mnzake. Mzinda udzamenyana ndi mzinda unzake ndipo ufumu udzamenyana ndi ufumu unzake.+ 3 Anthu a mu Iguputo adzadabwa kwambiri+ ndipo ine ndidzasokoneza zolinga za dzikolo.+ Iwo adzafunsira kwa milungu yopanda pake,+ kwa anthu amatsenga, kwa olankhula ndi mizimu ndiponso kwa olosera zam’tsogolo.+ 4 Ndidzapereka Iguputo m’manja mwa mbuye wankhanza ndipo mfumu imene idzawalamulire idzakhala yamphamvu,”+ akutero Ambuye woona, Yehova wa makamu.
5 Madzi adzauma m’nyanja, ndipo mtsinje udzakhala wopanda madzi ndi wouma.+ 6 Mitsinje idzanunkha. Ngalande za ku Iguputo zochokera mumtsinje wa Nailo zidzaphwa ndipo zidzauma.+ Bango+ ndi udzu* zidzafota. 7 Madambo a m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo, malo othera mtsinje wa Nailo, ndi malo onse obzala mbewu m’mphepete mwa mtsinjewo, adzauma.+ Zomera za m’mphepete mwa mtsinjewo zidzauma ndipo zidzauluzika ndi mphepo. 8 Asodzi a nsomba adzalira ndipo onse oponya mbedza mumtsinje wa Nailo adzamva chisoni. Ngakhale oponya maukonde ophera nsomba pamadziwo adzalefuka.+ 9 Anthu amene amagwiritsira ntchito fulakesi*+ wopalapala pa ntchito yawo adzachita manyazi. Anthu owomba nsalu yoyera adzachitanso manyazi. 10 Anthu ake owomba nsalu+ adzavutika maganizo. Anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzamva chisoni mumtima.
11 Akalonga a ku Zowani+ ndi opusa ndithu. Malangizo a anthu anzeru ochokera pakati pa alangizi a Farao, ndi osathandiza.+ Kodi anthu inu mudzamuuza bwanji Farao kuti: “Ine ndine mwana wa anthu anzeru, mwana wa mafumu akale”? 12 Kodi anthu ako anzeruwo ali kuti?+ Ngati akudziwa, akuuze zimene Yehova wa makamu wakonza zokhudza Iguputo.+ 13 Akalonga a ku Zowani achita zopusa.+ Akalonga a ku Nofi+ anyengezedwa. Atsogoleri+ a mafuko achititsa Iguputo kuyenda uku ndi uku. 14 Yehova waika mzimu wachisokonezo pakati pa dzikolo.+ Atsogoleri awo achititsa Iguputo kuyenda uku ndi uku m’zochita zake zonse, ngati munthu woledzera amene akuterereka m’masanzi ake.+ 15 Sipadzakhala chilichonse choti Iguputo achite, choti mutu kapena mchira komanso mphukira ndi udzu zichite.+
16 M’tsiku limenelo, Aiguputo adzakhala ngati akazi. Iwo adzanjenjemera+ ndi kuchita mantha, chifukwa Yehova wa makamu adzawatambasulira dzanja lake.+ 17 Dziko la Yuda lidzakhala chinthu choopseza Iguputo.+ Aliyense amene wauzidwa za dzikolo, akuchita mantha chifukwa cha zimene Yehova wa makamu watsimikiza kuwachitira.+
18 M’tsiku limenelo, padzakhala mizinda isanu m’dziko la Iguputo+ yolankhula chinenero cha ku Kanani+ ndiponso yolumbira+ kwa Yehova wa makamu. Mzinda umodzi udzatchedwa Mzinda wa Chiwonongeko.
19 M’tsiku limenelo, m’dziko la Iguputo mudzakhala guwa lansembe la Yehova,+ ndipo m’malire mwake mudzakhala chipilala cha Yehova. 20 Zimenezi zidzakhala chizindikiro ndi umboni kwa Yehova wa makamu m’dziko la Iguputo,+ pakuti iwo adzalirira Yehova chifukwa cha anthu owapondereza,+ ndipo iye adzawatumizira mpulumutsi wamkulu amene adzawapulumutse.+ 21 Yehova adzadziwika bwino kwa Aiguputo,+ ndipo Aiguputowo adzamudziwa Yehova m’tsiku limenelo. Iwo adzapereka nsembe ndi mphatso+ ndiponso adzachita lonjezo kwa Yehova n’kulikwaniritsa.+ 22 Yehova adzakantha Iguputo.+ Adzamukantha n’kumuchiza,+ ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova.+ Iye adzamva kuchonderera kwawo ndipo adzawachiritsa.+
23 M’tsiku limenelo, padzakhala msewu waukulu+ wochokera ku Iguputo kupita ku Asuri. Anthu a ku Asuri adzapita ku Iguputo ndipo anthu a ku Iguputo adzapita ku Asuri. Aiguputo ndi Asuri adzatumikira Mulungu limodzi. 24 M’tsiku limenelo, Isiraeli adzakhala gawo limodzi mwa magawo atatu, pamodzi ndi Iguputo ndi Asuri,+ kutanthauza kuti adzakhala dalitso padziko lapansi,+ 25 popeza Yehova wa makamu adzawadalitsa+ n’kuwauza kuti: “Adalitsike Aiguputo anthu anga, Asuri+ ntchito ya manja anga, ndi Aisiraeli cholowa changa.”+