Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Philemon 1-25
  • Filimoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Filimoni
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Filimoni

Kwa Filimoni

1 Ine Paulo, mkaidi+ chifukwa cha Khristu Yesu, pamene ndili limodzi ndi Timoteyo+ m’bale wathu, ndikulembera iwe wokondedwa ndi wantchito mnzathu Filimoni,+ 2 mlongo wathu Apiya ndiponso msilikali mnzathu+ Arikipo,+ ndi mpingo umene umasonkhana m’nyumba mwako:+

3 Anthu inu, kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+

4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu wanga ndikamatchula za iwe m’mapemphero anga,+ 5 pamene ndikumva za chikondi ndi chikhulupiriro chimene uli nacho kwa Ambuye Yesu ndi kwa oyera onse.+ 6 Ndimachita zimenezi kuti upitirize kusonyeza ena chikhulupiriro,+ chifukwa ukudziwa kuti ifeyo tinalandira zinthu zabwino zambiri zokhudzana ndi Khristu. 7 Chikondi chako m’bale chandisangalatsa ndi kundilimbikitsa kwambiri,+ chifukwa walimbikitsanso mitima ya oyera.+

8 Pa chifukwa chimenechi, ngakhale kuti mwa Khristu ndili ndi ufulu waukulu wa kulankhula moti nditha kukuuza+ zoyenera kuchita, 9 ndikukupempha mwachikondi,+ poona mmene ndililimu. Ineyo Paulo ndine wachikulire, komanso tsopano ndine mkaidi+ chifukwa cha Khristu Yesu. 10 Ndikukupempha za mwana wanga+ Onesimo,+ amene ndakhala bambo+ wake pamene ndili m’ndende. 11 Iye kale anali wopanda thandizo kwa iwe, koma tsopano ndi wothandiza kwa iwe ndi ine.+ 12 Ameneyu ndikumutumizanso kwa iwe. Ndithu, iye ndi wapamtima panga weniweni.+

13 Ndikanakonda kumusunga kuti m’malo mwa iwe,+ apitirize kunditumikira pamene ndili m’ndende+ chifukwa cha uthenga wabwino. 14 Koma sindikufuna kuchita kanthu mwa ine ndekha popanda chilolezo chako, kuti chabwino chimene ungachite chisakhale chokukakamiza, koma uchite mwa kufuna kwa mtima wako.+ 15 Mwina n’chifukwa chake anachoka kwa iwe kwa kanthawi, kuti udzakhale nayenso kwamuyaya. 16 Sukhala nayenso monga kapolo,+ koma woposa kapolo.+ Ukhala naye monga m’bale amene ine ndimamukonda kwambiri,+ ndipo iwe uyenera kumukonda koposa pamenepo popeza iye ndi kapolo wako ndi m’bale wako mwa Ambuye. 17 Choncho, ngati umandionadi kuti ndine mnzako,+ umulandire+ ndi manja awiri monga mmene ungalandirire ineyo. 18 Komanso ngati anakulakwira kanthu kalikonse kapena ngati ali nawe ngongole, ngongole imeneyo ikhale kwa ine. 19 Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa:+ Ndidzabweza ngongoleyo. Sindikufunikira kuchita kukuuza zimenezi, pajatu iwenso uli ndi ngongole kwa ine ya moyo wako. 20 Tandilola m’bale kuti ndipindule nawe mwa Ambuye: Ulimbikitse mtima wanga+ monga munthu wotsatira Khristu.

21 Ndikukulembera kalatayi pokhulupirira kuti uchita zimenezi. Ndikudziwa kuti uchita ngakhale zoposa zimene ndanenazi.+ 22 Komanso, ukonzeretu malo anga ogona,+ pakuti ndili ndi chikhulupiriro chakuti chifukwa cha mapemphero+ anu, ndimasulidwa+ kuti ndidzakutumikireni.

23 Epafura,+ mtumiki mnzanga mwa Khristu Yesu, akupereka moni. 24 Antchito anzanga, Maliko, Arisitako,+ Dema+ ndi Luka nawonso akupereka moni.

25 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu chifukwa cha mzimu umene mumaonetsa.+

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena