Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Titus 1:1-3:15
  • Tito

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tito
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Tito

Kwa Tito

1 Ine Paulo, kapolo+ wa Mulungu ndi mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndili ndi chikhulupiriro chogwirizana ndi cha anthu osankhidwa+ ndi Mulungu. Komanso ndine wodziwa molondola+ choonadi+ chokhudza kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+ 2 kumene kwazikidwa pa chiyembekezo cha moyo wosatha,+ chomwe Mulungu amene sanganame,+ analonjeza kalekale.+ 3 Koma mu nthawi yake, anapangitsa mawu ake kuonekera kudzera mu ulaliki umene ndinapatsidwa+ mwa lamulo la Mpulumutsi wathu,+ Mulungu. 4 Ndikulembera Tito, mwana wanga+ weniweni m’chikhulupiriro chimodzi chomwe tili nacho:

Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere wa Mulungu Atate+ ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu,+ zikhale nawe.

5 Ndinakusiya ku Kerete+ kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike+ akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo+ amene ndinakupatsa. 6 Mkulu ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera,+ mwamuna wa mkazi+ mmodzi, wa ana okhulupirira ndi osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika.+ 7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera.+ Pokhala mtumiki*+ wa Mulungu, asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa,*+ wandewu,+ kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo.+ 8 Koma akhale wochereza alendo,+ wokonda zabwino, woganiza bwino,+ wolungama, wokhulupirika,+ wodziletsa,+ 9 wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso,+ kuti athe kulimbikitsa anthu ndi chiphunzitso cholondola+ ndiponso kudzudzula+ otsutsa.

10 Pakuti pali anthu ambiri osalamulirika, olankhula zopanda pake,+ ndi opotoza maganizo a ena, makamaka amene akusungabe mdulidwe+ pakati pa anthu amenewa. 11 N’kofunika kuwatseka pakamwa, pakuti anthu amenewa, pofuna kupeza phindu mwachinyengo,+ akuwonongabe mabanja athunthu+ mwa kuphunzitsa zinthu zimene sayenera kuphunzitsa. 12 Wina wa iwo, amenenso ndi mneneri wawo, ananena kuti: “Akerete ndi anthu abodza nthawi zonse, zilombo zakutchire zolusa,+ ndiponso alesi osusuka.”

13 Umboni umenewu ndi woona. Chifukwa cha zimenezi, pitiriza kuwadzudzula mwamphamvu,+ kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.+ 14 Asamasamale nthano zachiyuda+ ndi malamulo a anthu+ amene asiya choonadi.+ 15 Zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera.+ Koma kwa anthu oipitsidwa+ ndi opanda chikhulupiriro+ kulibe choyera, m’malomwake maganizo awo ndi chikumbumtima+ chawo n’zoipa. 16 Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu,+ koma amamukana ndi zochita zawo+ chifukwa ndi onyansa ndi osamvera, ndipo ndi osayenerera+ ntchito iliyonse yabwino.

2 Koma iwe pitiriza kulankhula zinthu zogwirizana ndi chiphunzitso cholondola.+ 2 Amuna achikulire+ akhale osachita zinthu mopitirira malire, opanda chibwana,+ oganiza bwino, achikhulupiriro cholimba,+ achikondi chachikulu, ndi opirira+ kwambiri. 3 Chimodzimodzinso akazi achikulire.+ Akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche,+ kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino, 4 kuti azikumbutsa akazi achitsikana kukonda amuna+ awo, kukonda ana+ awo, 5 kukhala oganiza bwino, oyera,+ ogwira ntchito zapakhomo, abwino ndi ogonjera+ amuna awo, kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.+

6 Mofanana ndi zimenezi, pitiriza kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.+ 7 M’zinthu zonse, ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino.+ Chiphunzitso+ chako chikhale chopanda chinyengo.+ Usonyeze kuti ndiwe wopanda chibwana. 8 Mawu ako akhale oyenera amene sangatsutsike,+ kuti munthu wotsutsa achite manyazi, ndipo asapeze choipa chotinenera nacho.+ 9 Akapolo+ azigonjera ambuye awo pa zonse+ ndipo aziwakondweretsa. Asamatsutsane nawo+ 10 kapena kuwabera,+ koma akhale okhulupirika pa chilichonse,+ kuti akometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi+ wathu Mulungu, m’zinthu zonse.

11 Pakuti Mulungu waonetsa+ kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene kumabweretsa chipulumutso+ kwa anthu, kaya akhale a mtundu wotani.+ 12 Zimenezi zatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu+ ndi zilakolako za dziko,+ koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu+ m’nthawi* ino.+ 13 Tizichita zimenezi pamene tikuyembekeza kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo+ chosangalatsa ndi kuonetsedwa kwaulemerero+ kwa Mulungu wamkuluyo ndiponso kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. 14 Iyeyo anadzipereka+ m’malo mwa ife kuti atilanditse+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse,+ kuti tikhale anthu akeake,+ odzipereka pa ntchito zabwino.+

15 Pitiriza kulankhula zimenezi, kulimbikitsa ndi kudzudzula anthu mogwirizana ndi ulamuliro wonse umene wapatsidwa.+ Munthu aliyense asakuderere.+

3 Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera+ ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.+ Komanso akhale okonzekera ntchito iliyonse yabwino.+ 2 Asamanenere zoipa munthu aliyense, ndipo asakhale aukali.+ Koma akhale ololera,+ ndi ofatsa kwa anthu onse.+ 3 Pakuti ngakhale ife nthawi inayake tinali opanda nzeru, osamvera, osocheretsedwa, akapolo a zilakolako ndi zosangalatsa zosiyanasiyana, ochita zoipa, akaduka, onyansa ndiponso achidani.+

4 Komatu Mpulumutsi+ wathu Mulungu, anaonetsa+ kukoma mtima+ ndi kukonda anthu. 5 Iye sanatero chifukwa cha ntchito+ zolungama zimene tinachita+ ayi. Koma malinga ndi chifundo+ chake, anatipulumutsa mwa kutisambitsa+ ndipo chifukwa chakuti tinasambitsidwa choncho, tinafika ku moyo+ watsopano. Komanso, anatipulumutsa potisandutsa atsopano mwa mzimu woyera.+ 6 Iye anatikhuthulira mzimu umenewu kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu,+ 7 kuti titayesedwa olungama+ mwa kukoma mtima kwake kwakukulu,+ tikhale olandira cholowa+ mogwirizana ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.+

8 Mawu amenewa ndi oona,+ ndipo ndikufuna kuti nthawi zonse uzinena zinthu zimenezi motsindika, kuti amene akukhulupirira Mulungu nthawi zonse aziganiza za mmene angapitirizire kuchita ntchito zabwino.+ Zinthu izi n’zabwino ndi zothandiza kwa anthu.

9 Koma iwe pewa mafunso opusa,+ kukumba mibadwo ya makolo,+ mikangano+ ndi kulimbana pa za Chilamulo,+ chifukwa zimenezi n’zosapindulitsa ndiponso n’zachabechabe. 10 Munthu wolimbikitsa mpatuko,+ usagwirizane+ nayenso utamudzudzula koyamba ndi kachiwiri,+ 11 podziwa kuti munthu wotero wapotozedwa ndipo amadziimba mlandu chifukwa akudziwa kuti akuchimwa.+

12 Ndikadzatuma Atema kapena Tukiko+ kwa iwe, udzachite chilichonse chotheka kuti udzandipeze ku Nikopoli, chifukwa ndaganiza zokakhala kumeneko nyengo yachisanuyi.+ 13 Zena, wodziwa Chilamulo uja, komanso Apolo, uwapatse zofunika zokwanira zapaulendo, kuti asasowe kanthu.+ 14 Koma abale athu aphunzire kugwira ntchito zabwino kuti athe kupeza zinthu zofunika,+ ndiponso kuti asakhale opanda phindu.+

15 Onse amene ali nane akupereka moni.+ Undiperekere moni kwa anthu amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro.

Kukoma mtima kwakukulu kukhale ndi inu nonse.+

Mawu ake enieni, “mtumiki woyang’anira nyumba.”

Kapena kuti, “munthu womwa mowa mwauchidakwa amene amakonda kulongolola ndi kuchita ndewu akaledzera.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena