Kwa Aheberi
1 Kalekale, Mulungu analankhula ndi makolo athu nthawi zambiri+ ndiponso m’njira zambiri kudzera mwa aneneri.+ 2 Kumapeto kwa masiku ano,+ iye walankhulanso kwa ife kudzera mwa Mwana wake,+ amene anamuika kuti akhale wolandira zinthu zonse monga cholowa.+ Kudzera mwa iyeyu, Mulungu analenga+ nthawi* zosiyanasiyana. 3 Iye amasonyeza ndendende mmene ulemerero wa Mulungu ulili+ ndipo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo,+ ndipo amachirikiza zinthu zonse mwa mawu ake amphamvu.+ Atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala pansi kudzanja lamanja+ la Wolemekezeka m’malo okwezeka.+ 4 Choncho iye wakhala woposa angelo,+ moti monga cholowa chake, walandira dzina+ lapamwamba kwambiri kuposa lawo.
5 Mwachitsanzo, kodi Mulungu anauzapo mngelo uti kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala atate wako”?+ Kapena kuti: “Ine ndidzakhala atate wake ndipo iye adzakhala mwana wanga”?+ 6 Koma ponena za nthawi imene adzatumize kachiwiri Mwana wake Woyamba kubadwayo+ padziko lapansi kumene kuli anthu, iye akuti: “Angelo+ onse a Mulungu amugwadire.”+
7 Ndiponso ponena za angelo, iye akuti: “Amapanga angelo ake kukhala mizimu, ndipo amapanganso antchito ake otumikira ena kukhala lawi la moto.”+ 8 Koma ponena za Mwana wake, iye akuti: “Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka muyaya,+ ndipo ndodo ya ufumu+ wako ndiyo ndodo yachilungamo.+ 9 Unakonda chilungamo ndipo unadana ndi kusamvera malamulo. N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, anakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu kuposa cha mafumu ena.”+ 10 Iye akunenanso kuti: “Inu Ambuye, pachiyambipo munaika maziko a dziko lapansi, ndipo kumwamba ndiko ntchito ya manja anu.+ 11 Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapo mpaka muyaya. Ndipo zonsezi zidzatha ngati mmene malaya akunja amathera.+ 12 Mudzapindapinda zinthu zimenezi ngati mkanjo,+ ndipo zidzasinthidwa ngati malaya akunja. Koma inu simudzasintha, ndipo zaka za moyo wanu sizidzatha.”+
13 Koma kodi ndi mngelo uti amene anamuuzapo kuti: “Khala kudzanja langa lamanja, kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako”?+ 14 Kodi angelo onse si mizimu+ yotumikira ena,+ yotumidwa kukatumikira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo?+
2 Ndiye chifukwa chake n’kofunika kuti tiganizire mozama, kuposa nthawi zonse, zinthu zimene tinamva,+ kuti tisatengeke pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro.+ 2 Pakuti ngati mawu amene angelo ananena+ analidi osagwedezeka, ndipo pa tchimo lililonse ndi kusamvera kulikonse, chilango chinaperekedwa mogwirizana ndi chilungamo,+ 3 tidzapulumuka bwanji+ ngati tanyalanyaza+ chipulumutso chachikulu chonchi?+ Ambuye wathu ndi amene anayamba kunena za chipulumutso chimenechi,+ ndipo anthu amene anamumva anatitsimikizira zimenezo.+ 4 Mulungu nayenso anachitira umboni za chipulumutsocho ndi zizindikiro, zinthu zodabwitsa, ntchito zamphamvu zosiyanasiyana+ komanso mwa kupereka mphatso zosiyanasiyana+ za mzimu woyera malinga ndi chifuniro chake.+
5 Pakuti dziko lapansi lokhalamo anthu limene likubweralo,+ limene ife tikunena, sanaliike pansi pa ulamuliro wa angelo. 6 Koma mboni ina inachitira umboni penapake, kuti: “Munthu ndani kuti muzimuganizira,+ kapena mwana wa munthu ndani kuti muzimusamalira?+ 7 Munamutsitsa pang’ono poyerekeza ndi angelo. Munamuveka ulemerero ndi ulemu+ monga chisoti chachifumu, ndipo munamuika kuti alamulire ntchito za manja anu.+ 8 Zinthu zonse munaziika pansi pa mapazi ake.”+ Popeza kuti anaika zinthu zonse pansi pa mwana wake,+ Mulungu sanasiye kanthu kalikonse, osakaika pansi pa mwana wakeyo.+ Komabe, padakali pano sitikuona kuti zinthu zonse zili pansi pake.+ 9 Koma tikuona Yesu, amene pa nthawi ina anamutsitsa pang’ono poyerekeza ndi angelo.+ Tikumuona atamuveka ulemerero+ ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anazunzika mpaka imfa.+ Zimenezi zinamuchitikira kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.+
10 Zinthu zonse zilipo kuti zipereke ulemerero kwa Mulungu ndipo zinakhalapo kudzera mwa iye.+ Choncho pamene akuika ana ambiri pa ulemerero,+ n’koyenera kuti achititse Mtumiki Wamkulu+ wa chipulumutso chawo kukhala wangwiro kudzera m’masautso.+ 11 Pakuti onse, woyeretsayo ndi amene akuyeretsedwawo,+ amachokera kwa mmodzi.+ Pa chifukwa chimenechi, iye sachita manyazi kuwatcha “abale,”+ 12 pamene akunena kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani mwa kuimba nyimbo pakati pa mpingo.”+ 13 Komanso pamene akunena kuti: “Ndidzadalira iye.”+ Ndi kutinso: “Taonani! Ine ndi ana amene Yehova anandipatsa.”+
14 Chotero, popeza kuti “ana” amenewo onse ndi amagazi ndi mnofu, iyenso anakhala wamagazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake,+ awononge+ Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+ 15 Anachitanso zimenezi kuti amasule+ onse amene poopa imfa,+ anali mu ukapolo moyo wawo wonse.+ 16 Pakuti iye sakuthandiza angelo ngakhale pang’ono, koma akuthandiza mbewu ya Abulahamu.+ 17 Chotero, iye anayenera ndithu kukhala ngati “abale” ake m’zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu.+ Cholinga chake chinali choti apereke nsembe yophimba machimo+ kuti tikhalenso ogwirizana ndi Mulungu.+ 18 Popeza kuti iye mwini anavutika pamene anali kuyesedwa,+ amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.+
3 Chotero, abale athu oyera, amene muli nawo m’gulu la oitanidwa kumwamba,+ ganizirani za Yesu, mtumwi+ ndi mkulu wa ansembe amene tikumuvomereza.+ 2 Iye anali wokhulupirika+ kwa Mulungu amene anamuika kukhala mtumwi ndi mkulu wa ansembe, monga mmenenso Mose+ analili wokhulupirika m’nyumba yonse ya Mulungu.+ 3 Pakuti Yesu waonedwa kukhala woyenera ulemerero waukulu+ kuposa Mose, monganso mmene womanga+ nyumba amakhalira wolemekezeka kuposa nyumbayo.+ 4 N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.+ 5 Ndipo Mose monga wantchito+ anali wokhulupirika m’nyumba yonse ya Mulungu. Utumiki wakewo unali umboni wa zinthu zimene zidzalankhulidwe m’tsogolo.+ 6 Koma Khristu monga Mwana+ wa mwiniwake wa nyumbayo, anali kuyang’anira nyumba ya Mulungu mokhulupirika. Ife ndife nyumba ya Mulunguyo,+ ngati tagwira mwamphamvu ufulu wathu wa kulankhula ndi kupitirizabe kunyadira chiyembekezocho mpaka mapeto.+
7 Pa chifukwa chimenechi, mzimu woyera+ ukunena kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ 8 musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima,+ ngati mmene zinalili pa tsiku la mayeso+ m’chipululu.+ 9 M’chipululumo, makolo anu anandiyesa ndi mayesero, ngakhale kuti anali ataona ntchito zanga+ kwa zaka 40.+ 10 Pa chifukwa chimenechi ndinanyansidwa ndi m’badwo umenewo, ndipo ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera,+ ndipo sadziwa njira zanga.’+ 11 Choncho ndinalumbira mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa+ mu mpumulo wanga.’”+
12 Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+ 13 M’malomwake, pitirizani kudandaulirana+ tsiku ndi tsiku, nthawi iliyonse imene mukuti “Lero,”+ kuopera kuti chinyengo+ champhamvu cha uchimo chingaumitse mtima wa wina wa inu. 14 Pakuti kwenikweni timachita nawo zimene Khristu akuchita,+ ngati zinthu zimene tinali kudalira pa chiyambi, tazigwira mwamphamvu mpaka mapeto.+ 15 Tichite zimenezi pamene Malemba akunena kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima.”+
16 Kodi paja ndi ndani amene anamva koma n’kupsetsa mtima Mulungu?+ Kodi si anthu onse amene anatuluka m’dziko la Iguputo motsogoleredwa ndi Mose?+ 17 Komanso, kodi Mulungu ananyansidwa ndi ndani kwa zaka 40?+ Kodi sananyansidwe ndi anthu amene anachimwa aja, amene anafera m’chipululu?+ 18 Nanga kodi analumbirira+ ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Kodi si omwe aja amene anachita zosamvera?+ 19 Choncho, tikuona kuti sakanatha kulowa mu mpumulowo chifukwa anali opanda chikhulupiriro.+
4 Chotero, popeza lonjezo lolowa mu mpumulo wake lidakalipo,+ samalani kuopera kuti pa nthawi ina, wina wa inu angalephere kukwaniritsa zofunika kuti akalowe mu mpumulowo.+ 2 Uthenga wabwino unalengezedwa kwa ife,+ monga mmenenso unalengezedwera kwa makolo athu.+ Koma mawu amene iwo anamva sanapindule nawo,+ chifukwa sanakhale ndi chikhulupiriro+ ngati cha amene anamvera mawuwo.+ 3 Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mu mpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira+ mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa+ mu mpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti ntchito zake zinali zitatha+ kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa.*+ 4 Pakuti penapake, ponena za tsiku la 7, anati: “Ndipo Mulungu anapuma pa ntchito zake zonse pa tsiku la 7.”+ 5 Panonso akunena kuti: “Sadzalowa mu mpumulo wanga.”+
6 Choncho, popeza kuti ena ayenerabe kulowa mu mpumulo umenewo, ndipo amene anali oyamba kuwalalikira uthenga wabwino+ sanalowemo chifukwa cha kusamvera,+ 7 iye wapatulanso tsiku lina chifukwa wagwiritsa ntchito mawu akuti “Lero” mu salimo la Davide, pambuyo pa nthawi yaitali kwambiri. Izi zikugwirizana ndi zimene tanena kale zija kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu.”+ 8 Pakuti ngati Yoswa+ anawalowetsa m’malo ampumulo,+ Mulungu sakananenanso pambuyo pake+ za tsiku lina. 9 Chotero mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.+ 10 Munthu amene walowa mu mpumulo wa Mulungu,+ ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake,+ monga mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake.
11 Chotero, tiyeni tichite chilichonse chotheka kuti tilowe mu mpumulo umenewo, kuopera kuti wina angagwe ndi kutengera chitsanzo cha kusamvera cha makolo athuwo.+ 12 Pakuti mawu+ a Mulungu ndi amoyo+ ndi amphamvu,+ ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.+ Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo+ ndi mzimu,+ komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.+ 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
14 Chotero, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba,+ tiyeni tipitirize kulengeza chikhulupiriro chathu mwa iye.+ 15 Pakuti mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni+ pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+ 16 Choncho, tiyeni tiyandikire mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu ndipo tipemphere kwa Mulungu+ ndi ufulu wa kulankhula,+ kuti atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.+
5 Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa mwa anthu amaikidwa kuti achite utumiki wa Mulungu m’malo mwa anthu,+ kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.+ 2 Amakhala woleza mtima pochita zinthu ndi anthu osadziwa kanthu ndi olakwa, chifukwa iyenso ndi wofooka.+ 3 Ndipo chifukwa cha zimenezo, amafunika kupereka nsembe za machimo ake, monga mmene amaperekera nsembe za machimo a anthu onse.+
4 Komanso, munthu amalandira ulemu umenewu, osati mwa kufuna kwake,+ koma mwa kuchita kuitanidwa ndi Mulungu,+ monga mmene anaitanira Aroni.+ 5 Zilinso chimodzimodzi ndi Khristu. Iye sanadzipatse yekha ulemerero+ mwa kudziika yekha kukhala mkulu wa ansembe.+ Koma amene anamupatsa+ ulemerero umenewo ndi amene analankhula zokhudza iyeyu kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala atate wako.”+ 6 Monga mmene akuneneranso penapake kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”+
7 Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha,+ kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula+ komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.+ 8 Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo.+ 9 Ndipo atakhala wangwiro,+ anakhala ndi udindo wopereka chipulumutso chamuyaya+ kwa onse omumvera,+ 10 chifukwa watchulidwa mwachindunji ndi Mulungu kuti ndi mkulu wa ansembe monga mwa unsembe wa Melekizedeki.+
11 Tili ndi zambiri zoti tinene zokhudza iyeyu koma zovuta kuzifotokoza chifukwa chakuti inu mumachedwa kumvetsa zinthu.+ 12 N’zoona kuti munayenera kukhala aphunzitsi+ pofika nthawi ino. Koma sizili choncho, ndipo mukufunikanso wina woti akuphunzitseni mfundo zoyambirira+ za m’mawu opatulika a Mulungu,+ kuyambira pa chiyambi. Inu mwakhala ngati munthu wofunika mkaka, osati chakudya chotafuna.+ 13 Pakuti aliyense woyamwa mkaka sadziwa mawu a chilungamo, chifukwa adakali kamwana.+ 14 Koma chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu, amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira,+ aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.+
6 Pa chifukwa chimenechi, pamene tasiya chiphunzitso choyambirira+ cha Khristu+ tsopano, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.+ Tisayambe kuyalanso maziko,+ amene ndi kulapa ntchito zakufa,+ chikhulupiriro mwa Mulungu,+ 2 chiphunzitso chokhudza ubatizo,+ kuika manja,+ kuuka kwa akufa+ ndi chiweruzo chamuyaya.+ 3 Mulungu akalola, tiyesetsadi mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.+
4 Pali anthu amene Mulungu anawaunikira,+ amene analawa mphatso yaulere yakumwamba,+ amene analandira mzimu woyera,+ 5 amene analawa+ mawu abwino a Mulungu ndi zotsatira za mphamvu zimene Mulungu adzaonetse m’nthawi* imene ikubwerayo,+ 6 koma tsopano anagwa.+ Anthu amenewa n’zosatheka kuwadzutsanso kuti alape.+ N’zosatheka chifukwa chakuti anthu amenewa akupachika kachiwiri Mwana wa Mulungu ndi kumunyoza poyera.+ 7 Mwachitsanzo, nthaka imamwa madzi a mvula imene imagwera panthakapo kawirikawiri. Kenako imatulutsa zomera zimene zimapindulitsa amene ailima.+ Nthaka imeneyi imalandiranso dalitso kuchokera kwa Mulungu. 8 Koma ikatulutsa minga ndi mitula, imakanidwa ndipo imatsala pang’ono kutembereredwa.+ Mapeto ake imatenthedwa.+
9 Komabe ngakhale kuti tikulankhula motere, ndife otsimikiza kuti kwa inu okondedwa, zinthu zili bwino kwambiri kuposa amene anagwa aja. Muli ndi zinthu zabwino kwambiri zobweretsa chipulumutso. 10 Pakuti Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake,+ mwa kutumikira oyera+ ndipo mukupitiriza kuwatumikira. 11 Koma tikufuna kuti aliyense wa inu apitirize kuonetsa khama limene anali nalo poyamba, kuti chiyembekezo+ chanu chikhale chotsimikizika+ mpaka mapeto.+ 12 Pitirizani kuchita zimenezi kuti musakhale aulesi,+ koma mukhale otsanzira+ anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.+
13 Pamene Mulungu analonjeza Abulahamu,+ analumbira pa dzina lake+ chifukwa panalibe wina wamkulu kwa iye amene akanamulumbirira. 14 Iye anati: “Kudalitsa, ndidzakudalitsa ndithu, ndipo ndidzakuchulukitsadi.”+ 15 Choncho Abulahamu ataonetsa kuleza mtima, analandira lonjezo limeneli.+ 16 Pakuti anthu polumbira amatchula winawake wamkulu kwa iwo,+ ndipo lumbiro lawo limathetsa mkangano uliwonse, chifukwa kwa iwo lumbiro ndi chotsimikizira chalamulo.+ 17 Mofanana ndi zimenezi, Mulungu pofuna kuwatsimikizira kwambiri anthu olandira lonjezolo monga cholowa chawo,+ kuti chifuniro chake n’chosasinthika,+ anachita kulumbira pa zimene analonjezazo. 18 Anachita zimenezo kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, zimene chifukwa cha zinthu zimenezo n’zosatheka kuti Mulungu aname,+ ife amene tathawira kumalo otetezeka tilimbikitsidwe kwambiri, kuti tigwire mwamphamvu chiyembekezo+ chimene chaikidwa patsogolo pathu. 19 Chiyembekezo+ chimene tili nachochi chili ngati nangula* wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika. Chiyembekezo chimenechi chimatilowetsa mkati, kuseri kwa nsalu yotchinga,+ 20 kumene Yesu, yemwe ndi kalambulabwalo anakalowa chifukwa cha ife.+ Iyeyu wakhala mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.+
7 Melekizedeki ameneyu, mfumu ya mzinda wa Salemu, analinso wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.+ Iyeyu ndi amene anachingamira Abulahamu pochokera kokagonjetsa mafumu, ndipo anamudalitsa.+ 2 Abulahamu anapereka chakhumi cha zinthu zonse kwa iyeyu.+ Tikamasulira dzina lakeli, iye choyamba ndi “Mfumu Yachilungamo,” kenako, mfumu ya Salemu,+ kutanthauza kuti, “Mfumu Yamtendere.” 3 Popeza kuti analibe bambo, analibe mayi, analibe mzere wa mibadwo ya makolo ndipo tsiku limene anabadwa+ komanso limene anamwalira silikudziwika, koma anamuchititsa kuti afanane ndi Mwana wa Mulungu,+ iye ndi wansembe kwamuyaya.+
4 Choncho mungaone kuti munthuyu anali wofunika kwambiri. Moti ngakhale kholo lathu Abulahamu, linapereka kwa iye chakhumi pa zinthu zabwino kwambiri zimene anafunkha.+ 5 Zoonadi, amuna ochokera mwa ana aamuna a Levi,+ amene amalandira udindo wa unsembe, amalamulidwa kulandira zakhumi+ kuchokera kwa anthu+ malinga ndi Chilamulo. Izi zikutanthauza kuti, amalandira zakhumizo kuchokera kwa abale awo, ngakhale kuti abale awowo anachokera m’chiuno mwa Abulahamu.+ 6 Koma munthu amene sanachokere mumzere wobadwira+ wa Levi analandira chakhumi kwa Abulahamu,+ ndipo anadalitsa munthu amene anali ndi malonjezo.+ 7 Tsopano, palibe angatsutse kuti wamng’ono amadalitsidwa ndi wamkulu.+ 8 Alevi anali kulandira zakhumi ndipo ndi anthu oti amafa. Koma munthu wina amene analandira zakhumi,+ Malemba amamuchitira umboni kuti ali moyo.+ 9 Ndiponso, mwina ndifotokoze kuti, kudzera mwa Abulahamu, ngakhale Levi amene amalandira zakhumi, anapereka zakhumi. 10 Izi zinachitika m’njira yakuti iye anali adakali m’chiuno+ mwa kholo lake pamene Melekizedeki anakumana ndi kholo lakelo.+
11 Ndiyeno, ngati zikanakhala zothekadi kuti munthu akhale wangwiro+ kudzera mu unsembe wa Alevi,+ kodi pakanafunikanso kuti pakhale wansembe wina+ monga mwa unsembe wa Melekizedeki+ osati monga mwa unsembe wa Aroni? (Unsembe wa Alevi unali mbali ya Chilamulo pamene chinaperekedwa kwa anthu.)+ 12 Tsopano popeza kuti unsembewo ukusinthidwa,+ ndiye kuti chilamulonso chifunika kusintha.+ 13 Pakuti munthu amene akufotokozedwa ndi zinthu zimene zatchulidwazi ndi wa fuko lina,+ ndipo palibe aliyense wa fuko limenelo amene anatumikirapo paguwa lansembe.+ 14 Tonse tikudziwa kuti Ambuye wathu anatuluka m’fuko la Yuda,+ ndipo ponena za fuko limeneli Mose sanatchulepo chilichonse chokhudza ansembe.
15 Ndipo kwa ife n’zoonekeratu kwambiri kuti pakhalanso wansembe wina+ wofanana ndi Melekizedeki.+ 16 Iyeyu wakhala wotero, osati malinga ndi zofunika za chilamulo, chimene chimadalira zinthu za padziko lapansi,+ koma malinga ndi mphamvu imene imapatsa moyo wosakhoza kuwonongeka.+ 17 Pakuti Malemba amachitira umboni kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”+
18 Ndithudi, ndiye kuti malamulo oyambawo akuchotsedwa chifukwa chakuti ndi ofooka+ ndiponso operewera.+ 19 Pakuti Chilamulo sichinapangitse chilichonse kukhala changwiro,+ koma chiyembekezo+ chabwino kwambiri chimene anabweretsa kuwonjezera pa Chilamulocho, chinachita zimenezo. Ife tikuyandikira kwa Mulungu chifukwa cha chiyembekezo chimenecho.+ 20 Komanso zimenezi sizinachitike popanda lumbiro. 21 (Pakuti pali amuna ena amene akhala ansembe popanda lumbiro, koma pali mmodzi amene wakhala wansembe mwa lumbiro. Lumbiro limeneli ndi la Iye amene ananena za wansembeyo kuti: “Yehova walumbira+ (ndipo sadzasintha maganizo) kuti, ‘Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya.’”)+ 22 Pa chifukwa chimenecho, Yesu wakhala chikole cha pangano labwino koposa.+ 23 Ndiponso, panayenera kukhala ansembe ambiri olowana m’malo+ chifukwa imfa+ inali kuwaletsa kupitiriza unsembe wawo. 24 Koma iye chifukwa chokhala ndi moyo kosatha,+ palibe omulowa m’malo pa unsembe wake. 25 Ndiye chifukwa chake iye akhoza kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye, chifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.+
26 Pakuti mkulu wa ansembe ngati ameneyu ndiyedi wotiyenerera.+ Iye ndi wokhulupirika,+ wosalakwa,+ wosaipitsidwa,+ wosiyana ndi anthu ochimwa,+ ndipo wakwera pamwamba kwambiri kuposa kumwamba.+ 27 Iye safunikira kupereka tsiku ndi tsiku+ nsembe za machimo ake choyamba,+ kenako za anthu ena, monga mmene amachitira akulu a ansembe.+ (Iye anachita zimenezi kamodzi+ kokha pamene anadzipereka yekha nsembe.+ Nsembe imene anapereka motereyi ithandiza anthu mpaka muyaya.) 28 Chilamulo chimaika amuna okhala ndi zofooka+ kukhala akulu a ansembe.+ Koma mawu a lumbiro+ amene ananenedwa pambuyo pa Chilamulo anaika Mwana, amene anakhala wangwiro+ kosatha.
8 Ndiye kunena za zinthu zimene tikukambiranazi, mfundo yaikulu ndi iyi: Tili ndi mkulu wa ansembe+ ngati ameneyu, ndipo iye wakhala pansi kumwamba, kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka.+ 2 Iye ndi wantchito wotumikira ena wa m’malo oyerawo+ komanso m’chihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova,+ osati munthu.+ 3 Pakuti mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka zonse ziwiri, mphatso ndi nsembe.+ Ndiye chifukwa chake kunali kofunika kuti uyunso akhale ndi chinachake chopereka.+ 4 Choncho, iye akanakhalabe padziko lapansi, sakanakhala wansembe,+ popeza amuna opereka mphatsozo malinga ndi Chilamulo, alipo kale. 5 Koma amuna amenewo akuchita utumiki wopatulikawo m’chifaniziro+ ndi mu mthunzi+ wa zinthu zakumwamba. Izi zinaonekera mu lamulo limene Mulungu anapatsa Mose, atatsala pang’ono kumanga chihema.+ Lamulo lake linali lakuti:+ “Uonetsetse kuti wapanga zinthu zonse motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa m’phiri.”+ 6 Koma tsopano Yesu walandira ntchito yapamwamba kwambiri yotumikira ena, moti wakhalanso mkhalapakati+ wa pangano labwino kwambiri,+ limene lakhazikitsidwa mwalamulo pa malonjezo abwinonso.+
7 Pangano loyamba lija likanakhala lopanda zolakwika, sipakanafunikanso pangano lachiwiri.+ 8 Pakuti iye akuimba anthu mlandu pamene akunena kuti: “‘Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachita pangano latsopano ndi nyumba ya Isiraeli komanso ndi nyumba ya Yuda,’ watero Yehova.+ 9 ‘Koma pangano+ limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo,+ chifukwa iwo sanapitirize kusunga pangano+ langalo moti ndinasiya kuwasamalira,’ watero Yehova.”+
10 “‘Pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa pangano loyamba lija ndi ili: Ndidzaika malamulo anga m’maganizo mwawo ndi kuwalemba m’mitima yawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo+ ndipo iwo adzakhala anthu anga,’+ watero Yehova.
11 “‘Munthu sadzaphunzitsa nzika inzake kapena m’bale wake kuti: “Um’dziwe Yehova!”+ Pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa,+ kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu. 12 Ine ndidzawachitira chifundo pa zochita zawo zosalungama, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.’”+
13 Ponena kuti “pangano latsopano,” iye wapanga loyambalo kukhala lotha ntchito.+ Tsopano pangano limene latha ntchito ndipo likukalamba, latsala pang’ono kufafanizika.+
9 Tsopano, pangano loyamba lija linali ndi malamulo ake a utumiki wopatulika+ ndiponso malo ake oyera a padziko lapansi.+ 2 Pakuti panamangidwa chipinda choyamba cha chihema.+ M’chipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo,+ ndi mitanda ya mkate woonetsedwa,+ ndipo chinali kutchedwa “Malo Oyera.”+ 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+ 4 Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe,+ ndi likasa la pangano.+ Likasa lonseli linali lokutidwa ndi golide.+ M’likasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana.+ Munalinso ndodo ya Aroni imene inaphuka ija,+ komanso miyala yosema+ ya pangano. 5 Koma pamwamba pa likasalo panali akerubi aulemerero+ amene zithunzithunzi zawo zinali kugwera pachivundikiro chophimba machimo.+ Koma ino si nthawi yofotokoza zinthu zimenezi mwatsatanetsatane.
6 Zinthu zimenezi zitakonzedwa mwa njira imeneyi, ansembe anali kulowa m’chipinda choyamba+ nthawi zonse kukachita mautumiki opatulika.+ 7 Koma m’chipinda chachiwiricho, mkulu wa ansembe yekha ndiye anali kulowamo kamodzi pa chaka,+ ndipo sanali kulowamo popanda kutenga magazi.+ Magaziwo anali kuwapereka chifukwa cha iye mwini,+ komanso chifukwa cha machimo a anthu amene anachita mosadziwa.+ 8 Chotero mzimu woyera ukuonetsa poyera kuti njira+ yolowera kumalo oyera amkatikati inali isanaonekere pamene chihema choyambacho chinalipo.+ 9 Chihema chimenecho chinali chifaniziro+ cha nthawi yoikidwiratu imene tsopano yafika,+ ndipo mogwirizana ndi chifanizirocho, zonse ziwiri, mphatso ndi nsembe zimaperekedwa.+ Komabe, zimenezi sizipangitsa munthu amene akuchita utumiki wopatulikayo kukhala wangwiro+ m’chikumbumtima chake.+ 10 M’malomwake, zimangokhudza zakudya,+ zakumwa,+ ndi miyambo yosiyanasiyana yoviika zinthu m’madzi.+ Zimenezo zinali zofunika za Chilamulo zokhudza zinthu zathupi,+ ndipo zinakhazikitsidwa kufikira nthawi yoikidwiratu yokonzanso zinthu.+
11 Komabe, pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe,+ wa zinthu zabwino zimene zakwaniritsidwa, anatero kudzera m’chihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti, sichili mbali ya chilengedwe chapansi pano.+ 12 Choncho iye analowa m’malo oyera amkatikati ndi magazi+ ake, osati ndi magazi a mbuzi kapena a ng’ombe zazing’ono zamphongo. Analowa kamodzi kokha m’malo oyera amkatikatiwo, ndipo anatilanditsa kwamuyaya.+ 13 Pakuti ngati magazi a mbuzi+ ndi a ng’ombe zamphongo+ komanso phulusa+ la ng’ombe yaikazi imene sinaberekepo, zimene amawaza nazo anthu oipitsidwa,+ zimawayeretsa mpaka kukhaladi oyera pamaso pa Mulungu,+ 14 kuli bwanji magazi+ a Khristu, amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu wamuyaya?+ Kodi magazi amenewo sadzayeretsa+ zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika+ kwa Mulungu wamoyo?
15 Chotero, ndiye chifukwa chake iye ali mkhalapakati+ wa pangano latsopano kuti anthu amene aitanidwa alandire lonjezo la cholowa chamuyaya.+ Izi zatheka chifukwa cha imfa yake, imene inali ngati dipo+ lawo lowamasula ku machimo amene iwo anali nawo m’pangano lakale lija.+ 16 Pakuti pamene pali pangano,+ m’poyeneranso kuti munthu wochita naye panganoyo afe. 17 Pakuti pangano limagwira ntchito ngati wina wafapo, popeza siligwira ntchito nthawi iliyonse pamene munthu wochita naye panganoyo ali ndi moyo. 18 Ndiye chifukwa chake ngakhale pangano loyamba+ lija silinakhazikitsidwe popanda magazi.+ 19 Pakuti pamene Mose anatchulira anthu onsewo lamulo lililonse malinga ndi Chilamulo,+ anatenga magazi a ng’ombe zazing’ono zamphongo ndi magazi a mbuzi, pamodzi ndi madzi, ubweya wa nkhosa wofiira kwambiri, ndi timitengo ta hisope,+ n’kuwaza bukulo ndi anthu onse. 20 Iye anati: “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulani kuti mulisunge.”+ 21 Ndipo anawazanso magazi aja pachihema+ ndi paziwiya zonse zogwiritsa ntchito potumikira ena.+ 22 Inde, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi+ malinga ndi Chilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi+ anthu sangakhululukidwe machimo awo.+
23 Chotero kunali kofunikira kuti zifaniziro+ za zinthu zakumwamba ziyeretsedwe m’njira imeneyi,+ koma zinthu zakumwamba zenizenizo ziyeretsedwe ndi nsembe zabwino kuposa nsembe zoterezi. 24 Pakuti Khristu sanalowe m’malo oyera amkatikati opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Tsopano ali kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.+ 25 Iye sanapite kumwambako kuti azikadzipereka nsembe mobwerezabwereza, monga mmene mkulu wa ansembe amachitira. Mkulu wa ansembe amalowa m’malo oyera amkatikati+ chaka ndi chaka+ atatenga magazi a nyama osati ake. 26 Zikanatero, akanavutika mobwerezabwereza kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa.+ Koma tsopano iye waonekera+ kamodzi+ kokha pa mapeto a nthawi* zino+ kuti achotse uchimo kudzera mu nsembe yake.+ 27 Monga mmene zilili ndi anthu kuti amayembekezera+ kufa kamodzi kokha, kenako n’kudzalandira chiweruzo,+ 28 n’chimodzimodzinso Khristu. Iye anaperekedwa nsembe kamodzi+ kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri.+ Ndipo nthawi yachiwiri+ imene adzaonekere+ sadzaonekera n’cholinga chochotsa uchimo.+ Anthu amene akumuyembekezera ndi mtima wonse kuti awapulumutse ndi amene adzamuone.+
10 Popeza Chilamulo ndicho mthunzi chabe+ wa zinthu zabwino zimene zikubwera osati zinthu zenizenizo, ndiye kuti anthu wamba sangachititse anthu amene amalambira Mulungu kukhala angwiro. Iwo sangathe kuchita zimenezi mwa nsembe zimodzimodzizo zimene amapereka mosalekeza chaka ndi chaka.+ 2 Zikanakhala choncho, kodi nsembezo sakanasiya kuzipereka? Akanasiya chifukwa chakuti anthu ochita utumiki wopatulika, amene akanayeretsedwa kwathunthu kamodzi n’kamodziwo, sakanakhalanso ndi chikumbumtima chakuti ndi ochimwa.+ 3 Koma mosiyana ndi zimenezo, chaka ndi chaka nsembe zimenezi zimawakumbutsa za machimo awo.+ 4 Pakuti n’kosatheka kuti magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.+
5 Chotero pobwera m’dziko iye anati: “‘Nsembe ndiponso zopereka simunazifune,+ koma munandikonzera thupi.+ 6 Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.’+ 7 Ndiyeno ndinati, ‘Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine)+ kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’”+ 8 Choyamba atanena kuti: “Nsembe, zopereka, nsembe zopsereza zathunthu, ndi nsembe zamachimo simunazifune kapena kuzivomereza,”+ nsembe zimene zimaperekedwa malinga ndi Chilamulo,+ 9 ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri.+ 10 Mwa “chifuniro”+ chimenecho, tayeretsedwa+ kudzera m’thupi la Yesu Khristu loperekedwa nsembe+ kamodzi+ kokha.
11 Komanso, wansembe aliyense amaima pamalo ake+ kuti achite ntchito yotumikira ena ndi kupereka nsembe zimodzimodzizo mobwerezabwereza,+ popeza zimenezi sizingachotseretu machimo.+ 12 Koma munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo kwamuyaya,+ ndipo anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu.+ 13 Kuyambira pamenepo, akuyembekezera kufikira pamene adani ake adzaikidwe monga chopondapo mapazi ake.+ 14 Iye akuchititsa anthu amene akuyeretsedwa kukhala angwiro kwamuyaya,+ kudzera mu nsembe imodzi yokha basi.+ 15 Komanso, mzimu woyera+ nawonso ukuchitira umboni kwa ife, chifukwa utanena kuti: 16 “‘Pangano limene ndidzapanga nawo pambuyo pa pangano loyamba lija ndi ili: Ndidzaika malamulo anga m’mitima yawo ndi kuwalemba m’maganizo mwawo,’ watero Yehova,”+ 17 pambuyo pake ukunenanso kuti: “Ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo komanso zochita zawo zosonyeza kusamvera malamulo.”+ 18 Tsopano, pamene zimenezi zakhululukidwa,+ nsembe yamachimo si yofunikanso.+
19 Chotero abale, ndife olimba mtima chifukwa tikugwiritsa ntchito njira yolowera+ m’malo oyera+ kudzera m’magazi a Yesu. 20 Iye ndi amene anatikhazikitsira njira imeneyi monga njira yatsopano ndi yamoyo, yodutsa nsalu yotchinga,+ imene ndi thupi lake.+ 21 Popeza ndife olimba mtima chotero, komanso popeza kuti tili ndi wansembe wamkulu kwambiri woyang’anira nyumba ya Mulungu,+ 22 tiyeni timufikire Mulungu ndi mitima yoona. Tichite zimenezi tilibe chikayikiro chilichonse komanso tili ndi chikhulupiriro, pakuti mitima yathu yayeretsedwa* kuti isakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa m’madzi oyera.+ 23 Tiyeni tipitirize kulengeza poyera chiyembekezo+ chathu ndipo tisagwedezeke,+ pakuti amene anapereka lonjezo lija ndi wokhulupirika.+ 24 Ndipo tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane+ pa chikondi ndi ntchito zabwino.+ 25 Tisaleke kusonkhana pamodzi,+ monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane,+ ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.+
26 Pakuti ngati tikuchita machimo mwadala+ pambuyo podziwa choonadi molondola,+ palibe nsembe ina yotsala imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.+ 27 Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo,+ ndiponso pali nsanje yoyaka moto imene idzawononge otsutsawo.+ 28 Munthu aliyense amene wanyalanyaza chilamulo cha Mose amafa popanda kumuchitira chifundo, ngati anthu awiri kapena atatu apereka umboni.+ 29 Ndiye kuli bwanji munthu amene wapondaponda+ Mwana wa Mulungu, amene akuona magazi+ a pangano amene anayeretsedwa nawo ngati chinthu wamba, amenenso wanyoza mzimu+ wa Mulungu, yemwe amasonyeza kukoma mtima kwakukulu? Munthu ameneyu akuyenera kulandira chilango chachikulu kwambiri.+ 30 Pakuti timamudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.”+ Ndiponso: “Yehova adzaweruza anthu ake.”+ 31 Kulandira chilango chochokera kwa Mulungu wamoyo n’chinthu choopsa.+
32 Komabe, pitirizani kukumbukira masiku akale. Mutalandira kuwala kochokera kwa Mulungu m’masiku amenewo,+ munapirira mayesero aakulu ndi masautso.+ 33 Nthawi zina munali kupirira potonzedwa ndi posautsidwa poyera ngati chionetsero m’bwalo la masewera.+ Ndipo nthawi zina munali kupirira pamene munamva zowawa limodzi ndi ena amene anali kukumana ndi zimenezo.+ 34 Pakuti munasonyeza chifundo kwa amene anali m’ndende, ndipo munalola mokondwa kuti katundu wanu alandidwe,+ podziwa kuti inuyo muli ndi chuma chabwino kuposa pamenepo ndiponso chokhalitsa.+
35 Chotero, musataye ufulu wanu wa kulankhula,+ umene udzabweretse mphoto yaikulu kwambiri.+ 36 Pakuti mukufunika kupirira,+ kuti mutachita chifuniro cha Mulungu,+ mudzalandire zimene Mulungu walonjeza.+ 37 Pakuti “kwatsala kanthawi kochepa kwambiri,”+ ndipo “amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa ayi.”+ 38 “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati wabwerera m’mbuyo, ine sindikondwera naye.”+ 39 Tsopano, ife si mtundu wa anthu obwerera m’mbuyo kupita kuchiwonongeko,+ koma mtundu wa anthu okhala ndi chikhulupiriro chosunga moyo.+
11 Chikhulupiriro+ ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa,+ umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.+ 2 Pakuti mwa chikhulupiriro, anthu a nthawi zakale anali ndi umboni wakuti Mulungu akukondwera nawo.+
3 Mwa chikhulupiriro, timazindikira kuti mwa mawu a Mulungu, nthawi* zosiyanasiyana+ anaziika m’malo mwake,+ moti zimene zikuoneka zatuluka m’zinthu zosaoneka.+
4 Mwa chikhulupiriro, Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yamtengo wapatali kuposa ya Kaini.+ Ndipo mwa chikhulupirirocho, anachitiridwa umboni kuti anali wolungama, pakuti Mulungu anachitira umboni+ kuti walandira mphatso zakezo. Komanso mwa chikhulupiriro chimenecho, ngakhale kuti anafa, iye akulankhulabe.+
5 Mwa chikhulupiriro, Inoki+ anasamutsidwa kuti asafe mozunzika, moti sanapezeke kwina kulikonse chifukwa Mulungu anamusamutsa.+ Pakuti asanasamutsidwe, Mulungu anamuchitira umboni kuti akukondwera naye.+ 6 Ndiponso, popanda chikhulupiriro+ n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.+ Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi,+ ndi kuti amapereka mphoto+ kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.+
7 Mwa chikhulupiriro, Nowa+ atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke,+ anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa+ kuti banja lake lipulumukiremo. Mwa chikhulupiriro chimenecho, anatsutsa dziko,+ ndipo anakhala wolandira cholowa cha chilungamo,+ chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.
8 Mwa chikhulupiriro, Abulahamu+ ataitanidwa, anamvera ndi kupita kumalo amene anali kuyembekezera kuwalandira monga cholowa. Iye anapitadi, ngakhale sanadziwe kumene anali kupita.+ 9 Mwa chikhulupiriro, anakhala monga mlendo m’dziko la lonjezo ngati kuti akukhala m’dziko lachilendo.+ Ndipo anali kukhala m’mahema+ pamodzi ndi Isaki+ ndi Yakobo,+ anzake olandira nawo limodzi lonjezolo.+ 10 Pakuti anali kuyembekezera mzinda+ wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.+
11 Mwa chikhulupiriro, Sara+ nayenso analandira mphamvu yokhala ndi pakati* ngakhale kuti anali atapitirira zaka zobereka,+ chifukwa anaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupirika.+ 12 Choteronso, kuchokera mwa mwamuna mmodzi,+ amene anali ngati wakufa,+ kunabadwa ana ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba komanso osawerengeka ngati mchenga wa m’mbali mwa nyanja.+
13 Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro,+ ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo.+ Koma anawaona ali patali+ ndi kuwalandira, ndipo analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.+ 14 Pakuti onena zinthu zimenezi amapereka umboni wakuti akufunafuna mwakhama malo awoawo.+ 15 Koma akanakhala kuti anali kumangokumbukira malo amene anachokera,+ mpata wobwerera akanakhala nawo.+ 16 Koma tsopano akufunitsitsa malo abwino koposa, amene ndi malo akumwamba.+ Pa chifukwa chimenechi, Mulungu sachita nawo manyazi kuti azimuitana monga Mulungu wawo,+ pakuti iye wawakonzera mzinda.+
17 Mwa chikhulupiriro, pamene Abulahamu anayesedwa,+ zinali ngati wapereka kale Isaki nsembe. Choncho munthu ameneyu, amene analandira malonjezo mokondwera, anali wokonzeka kupereka nsembe mwana wake wobadwa yekha.+ 18 Anali wokonzeka kuchita zimenezo ngakhale kuti anali atauzidwa kuti: “Amene adzatchedwa ‘mbewu yako’ adzachokera mwa Isaki.”+ 19 Koma anadziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa kwa akufa.+ Ndipo iye anamulandiradi kuchokera kwa akufa m’njira ya fanizo.+
20 Mwa chikhulupiriro, Isaki nayenso anadalitsa Yakobo+ ndi Esau,+ pa nkhani yokhudza zinthu zimene zinali kubwera.
21 Mwa chikhulupiriro, Yakobo ali pafupi kufa,+ anadalitsa ana aamuna a Yosefe mmodzimmodzi,+ ndipo analambira Mulungu atatsamira pamutu wa ndodo yake.+
22 Mwa chikhulupiriro, Yosefe atayandikira mapeto a moyo wake, anatchula za kusamuka+ kwa ana a Isiraeli, ndipo anapereka lamulo lokhudza mafupa ake.+
23 Mwa chikhulupiriro, Mose atabadwa, makolo ake anamubisa kwa miyezi itatu,+ chifukwa anaona kuti mwanayo anali wokongola.+ Iwo sanaope lamulo+ la mfumu. 24 Mwa chikhulupiriro, Mose atakula+ anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao,+ 25 ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo. 26 Iye anachita zimenezi chifukwa anaona kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa* kukhala chuma chochuluka+ kuposa chuma cha Iguputo, pakuti anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire.+ 27 Mwa chikhulupiriro anachoka mu Iguputo,+ koma osati chifukwa choopa mfumu ayi,+ pakuti anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.+ 28 Mwa chikhulupiriro, iye anachita pasika+ ndiponso anawaza magazi pamafelemu a pakhomo,+ kuti wowonongayo asakhudze ana awo oyamba kubadwa.+
29 Mwa chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka Nyanja Yofiira ngati kuti akudutsa pamtunda pouma,+ koma Aiguputo atalimba mtima ndi kulowa panyanjapo, nyanjayo inawamiza.+
30 Mwa chikhulupiriro, makoma a Yeriko anagwa, atawazungulira masiku 7.+ 31 Mwa chikhulupiriro, Rahabi+ hule lija, sanawonongedwe limodzi ndi anthu amene anachita zinthu mosamvera, chifukwa iye analandira azondi mwamtendere.+
32 Nanga ndinenenso chiyani pamenepa? Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni,+ Baraki,+ Samisoni,+ Yefita,+ Davide,+ komanso Samueli+ ndi aneneri enanso.+ 33 Mwa chikhulupiriro, anthu amenewa anagonjetsa maufumu pa nkhondo,+ anachita chilungamo,+ analandira malonjezo+ ndiponso anatseka mikango pakamwa.+ 34 Anagonjetsa mphamvu ya moto,+ anathawa lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ analimba mtima pa nkhondo,+ ndiponso anagonjetsa magulu ankhondo a mayiko ena.+ 35 Akazi analandira akufa awo amene anauka kwa akufa.+ Koma anthu ena anazunzidwa chifukwa sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzauke kwa akufa, komwe ndi kuuka kwabwino kwambiri. 36 Ena analandira mayesero awo mwa kutonzedwa ndi kukwapulidwa, komanso kuposa pamenepo, mwa maunyolo+ ndi ndende.+ 37 Anaponyedwa miyala,+ anayesedwa,+ anachekedwa pakati ndi macheka, anaphedwa+ mwankhanza ndi lupanga, anayendayenda atavala zikopa za nkhosa+ ndi zikopa za mbuzi pamene anali osowa,+ pamene anali m’masautso+ komanso pamene anali kuzunzidwa.+ 38 Iwo anali abwino kwambiri, osayenera kukhala m’dziko lotereli. Anayenda uku ndi uku m’zipululu, m’mapiri, m’mapanga,+ ndi m’maenje a dziko lapansi.
39 Komabe onsewa, ngakhale kuti anachitiridwa umboni chifukwa cha chikhulupiriro chawo, sanaone kukwaniritsidwa kwa lonjezolo.+ 40 Zinatero chifukwa chakuti Mulungu anaoneratu chinthu chabwino kwambiri+ choti atipatse,+ kuti iwo+ asakhale angwiro+ popanda ife.+
12 Choncho, chifukwa chakuti tili ndi mtambo wa mboni+ waukulu chonchi wotizungulira, tiyeninso tivule cholemera chilichonse+ ndi tchimo limene limatikola mosavuta lija.+ Ndipo tithamange mopirira+ mpikisano+ umene atiikirawu.+ 2 Tichite zimenezi pamene tikuyang’anitsitsa Mtumiki Wamkulu+ ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu,+ Yesu. Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake,+ anapirira mtengo wozunzikirapo.* Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.+ 3 Ndithudi, ganizirani mozama za munthu amene anapirira malankhulidwe onyoza+ ngati amenewo a anthu ochimwa, amene mwa kulankhula koteroko anali kungodzivulaza okha. Ganizirani za munthu ameneyu kuti musatope ndiponso kuti musalefuke.+
4 Popitiriza mpikisano wanu wolimbana ndi tchimo limenelo, simunafikebe polimbana nalo mpaka kutaya magazi anu.+ 5 Ndipo mwaiwaliratu langizo lokudandaulirani limene limakutchani ana,+ lakuti: “Mwana wanga, usapeputse chilango* cha Yehova, kapena kutaya mtima pamene iye akukudzudzula.+ 6 Pakuti Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda, ndipo amakwapula aliyense amene iye amamulandira monga mwana wake.”+
7 Kupirira kumene mukupiriraku,+ mukupirira kuti chikhale chilango chanu. Mulungu akuchita nanu zinthu ngati ana ake.+ Ndi mwana wanji amene bambo ake samulanga?+ 8 Koma ngati simunalandire chilango chimene ena onse alandira, ndiye kuti ndinu ana apathengo,+ osati ana ake enieni. 9 Ndiponso, bambo athu otibereka, amene anali ndi thupi lanyama ngati lathuli anali kutilanga,+ ndipo tinali kuwalemekeza. Kuli bwanji ndi Atate wa moyo wathu wauzimu. Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?+ 10 Pakuti bambo athu otiberekawo, kwa masiku ochepa anali kutilanga malinga ndi zimene anaziona kuti n’zoyenera,+ koma Mulungu amatilanga kuti tipindule ndiponso kuti tikhale oyera ngati iyeyo.+ 11 Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+
12 Choncho limbitsani manja amene ali lende+ ndi mawondo olobodoka,+ 13 ndipo pitirizani kuwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo,+ kuti chiwalo chimene chavulala chisaguluke polumikizira, koma chichiritsidwe.+ 14 Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse,+ komanso yesetsani kukhala oyera+ chifukwa ngati munthu si woyera, sadzaona Ambuye.+ 15 Pochita zimenezo, muonetsetse kuti wina asalandidwe kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ komanso kuti pakati panu pasatuluke muzu wapoizoni+ woyambitsa mavuto, ndi kuti ambiri asaipitsidwe nawo.+ 16 Muonetsetsenso kuti pasakhale wadama kapena aliyense wosayamikira zinthu zopatulika, ngati Esau,+ amene anapereka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi chakudya chodya kamodzi kokha.+ 17 Mukudziwa kuti pambuyo pake, atafunanso kulandira dalitso monga cholowa chake,+ anamukanira.+ Pakuti ngakhale kuti anayesetsa ndi mtima wonse, kwinaku akugwetsa misozi,+ kuti bambo ake asinthe maganizo, sizinatheke.+
18 Pakuti simunafike paphiri limene mungathe kulikhudza,+ loyaka moto,+ lokhala ndi mtambo wakuda, mdima wandiweyani komanso lowombedwa ndi mphepo yamkuntho.+ 19 Simunafike paphiri limene panamveka kulira kwa lipenga+ ndi mawu a winawake akulankhula,+ amene anthu atawamva, anachonderera kuti asawauzenso mawu ena.+ 20 Pakuti lamulo lija linawakulira, lakuti: “Nyama iliyonse imene ingakhudze phirilo, iponyedwe miyala.”+ 21 Komanso, zimene anaona kumeneko zinali zoopsa kwambiri moti Mose anati: “Ndikuchita mantha ndipo ndikunjenjemera.”+ 22 Koma m’malomwake, inu mwafika kuphiri la Ziyoni+ ndi mzinda+ wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba,+ kumene kuli angelo miyandamiyanda,*+ 23 pamsonkhano wawo waukulu.+ Kumenenso kuli mpingo wa woyamba kubadwayo,+ mpingo wa iwo amene analembedwa+ kumwamba. Kumeneko kulinso Mulungu, Woweruza wa onse,+ ndiponso kuli moyo wauzimu wa olungama+ amene akhala angwiro.+ 24 Kulinso Yesu, mkhalapakati+ wa pangano latsopano,+ ndiponso magazi owaza,+ amene amalankhula m’njira yabwino kwambiri kuposa magazi a Abele.+
25 Samalani kuti musasiye kumvetsera wolankhulayo.+ Pakuti ngati amene analephera kumvera wopereka chenjezo la Mulungu padziko lapansi sanapulumuke,+ kuli bwanji ifeyo? Nafenso sitidzapulumuka tikachoka kwa iye amene amalankhula ali kumwamba.+ 26 Pa nthawiyo, mawu ake anagwedeza dziko lapansi,+ koma tsopano walonjeza kuti: “Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokhali.”+ 27 Tsopano, mawu akuti “Ndidzagwedezanso,” akusonyeza kuti zinthu zimene adzazigwedezezo zidzachotsedwa. Zimenezi ndi zinthu zimene zinapangidwa ndi winawake,+ ndipo adzazichotsa kuti zimene sizikugwedezeka zitsale.+ 28 Ndiye chifukwa chake, poona kuti tidzalandira ufumu umene sungagwedezeke,+ tiyeni tipitirize kulandira kukoma mtima kwakukulu, kuti kudzera m’kukoma mtima kwakukulu kumeneko, tichitire Mulungu utumiki wopatulika m’njira yovomerezeka, ndipo tiuchite moopa Mulungu komanso mwaulemu waukulu.+ 29 Pakuti Mulungu wathu alinso moto wowononga.+
13 Mupitirize kukonda abale.+ 2 Musaiwale kuchereza alendo,+ pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.+ 3 Kumbukirani amene ali m’ndende+ ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.+ Kumbukiraninso amene akuzunzidwa,+ popeza inunso mudakali m’thupi lanyama. 4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa,+ pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.+ 5 Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,+ koma mukhale okhutira+ ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”+ 6 Moti tikhale olimba mtima ndithu+ ndipo tinene kuti: “Yehova* ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”+
7 Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu.+ Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu. Ndipo pamene mukuonetsetsa zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani+ chikhulupiriro chawo.+
8 Yesu Khristu ali chimodzimodzi dzulo ndi lero, ndiponso mpaka muyaya.+
9 Musatengeke ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo.+ Ndi bwino kuti mtima ukhale wolimba chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu,+ osati chifukwa cha zakudya.+ Pakuti amene amatanganidwa ndi zakudyazo sakupindula nazo.
10 Ife tili ndi guwa lansembe limene ochita utumiki wopatulika kuchihema, alibe ulamuliro wodya za paguwapo.+ 11 Pakuti nyama zimene magazi ake, mkulu wa ansembe amalowa nawo m’malo oyera chifukwa cha machimo, amakazitentha kunja kwa msasa.+ 12 Zinalinso chimodzimodzi ndi Yesu. Kuti ayeretse+ anthu ndi magazi ake,+ anakavutikira kunja kwa chipata.+ 13 Chotero, tiyeni timutsatire kunja kwa msasako, titasenza chitonzo chimene iye anasenza.+ 14 Pakuti pamene tili pano, tilibe mzinda wokhazikika,+ koma ndi mtima wonse tikufunitsitsa mzinda umene ukubwerawo.+ 15 Kudzera mwa iye, tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu,+ yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.+ Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.+ 16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+
17 Muzimvera amene akutsogolera pakati panu+ ndipo muziwagonjera.+ Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu.+ Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.+
18 Pitirizani kutipempherera,+ pakuti tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.+ 19 Koma makamaka ndikukulimbikitsani kuchita zimenezi, kuti ndibwerere kwa inu mwamsanga.+
20 Tsopano, Mulungu wamtendere,+ amene anaukitsa kwa akufa+ m’busa wamkulu+ wa nkhosa+ wokhala ndi magazi a pangano losatha,+ Ambuye wathu Yesu, 21 akukonzekeretseni ndi chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake. Ndipo kudzera mwa Yesu Khristu, achite mwa ife zimene zili zokondweretsa pamaso pake.+ Kwa iye kukhale ulemerero kwamuyaya.+ Ame.
22 Tsopano, ndikukudandaulirani abale, chonde khalani oleza mtima pamene mukuwerenga mawu olimbikitsawa, chifukwa ndakulemberani kalatayi m’mawu ochepa.+ 23 Dziwani kuti m’bale wathu Timoteyo+ wamasulidwa, ndipo ngati angabwere posachedwapa, ndibwera naye limodzi kudzakuonani.
24 Mundiperekere moni kwa onse amene akutsogolera pakati panu,+ ndiponso kwa oyera ena onse. A ku Italiya+ akukupatsani moni.
25 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu+ kukhale nanu nonsenu.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “kuponya mbewu pansi.” Mbewuzo zikutanthauza ana a Adamu ndi Hava.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Nangula” ndi chinthu chimene amachimangirira kusitima ndipo amachiponya pansi pa nyanja kuti sitima ikaima isatengeke ndi mphepo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “yawazidwa,” kutanthauza kuti yawazidwa magazi a Yesu.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza kuti anatenga pakati kuti abereke mbewu.
Chigiriki, “Khristu.”
Onani Zakumapeto 9.
Onani Mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Kapena kuti, “masauzande makumimakumi.”
Onani Zakumapeto 2.