Nyimbo ya Solomo
1 Nyimbo yokoma kwambiri,+ nyimbo ya Solomo:+ 2 “Undipsompsone ndi milomo yako,+ chifukwa chikondi chimene umandisonyeza chimaposa vinyo kukoma kwake.+ 3 Mafuta+ ako odzola ndi onunkhira bwino. Dzina lako lili ngati mafuta othira pamutu.+ N’chifukwa chake atsikana amakukonda. 4 Nditenge,+ tiye tithawe! Chifukwatu mfumu yandipititsa m’zipinda zake zamkati.+ Tiye tikondwere ndi kusangalalira limodzi. Tiye tinene za chikondi chimene umandisonyeza osati za vinyo.+ M’pake kuti atsikana amakukonda.+
5 “Inu ana aakazi a ku Yerusalemu,+ ine ndine mtsikana wakuda ngati mahema a ku Kedara,+ koma wokongola ngati nsalu za mahema+ a Solomo. 6 Musandiyang’anitsitse chifukwa chakuti ndada, ndi dzuwatu landidetsali. Pakuti ana aamuna a mayi anga anandikwiyira. Choncho anandiika kuti ndiziyang’anira minda ya mpesa moti sindinathe kuyang’anira munda wangawanga wa mpesa.+
7 “Iwe amene mtima wanga umakukonda,+ tandiuza kumene umakadyetsera ziweto,+ kumene umakagonetsa ziweto masana. Kodi ndikhalirenji ngati mkazi amene wafunda nsalu ya namalira pakati pa magulu a ziweto za anzako?”
8 “Ngati iweyo sukudziwa, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse,+ tsatira mapazi a ziweto ndipo ukadyetse ana ako a mbuzi pafupi ndi mahema a abusa.”
9 “Kwa ine, wokondedwa wangawe+ ndiwe wokongola ngati hatchi* yaikazi ya pamagaleta* a Farao.+ 10 Masaya ako ndi okongola pakati pa tsitsi lako lomanga, ndipo khosi lako lovala mkandalo limaoneka bwino.+ 11 Ife tikupangira zokongoletsa zoti uzivala kumutu. Zokongoletsazo zikhala zozungulira, zagolide,+ zokhala ndi mikanda yasiliva.”
12 “Pamene mfumu yakhala patebulo lake lozungulira, fungo labwino la nado*+ wanga likumveka kwa wokondedwa wanga.+ 13 Wachikondi wanga ali ngati kathumba ka mule*+ kwa ine. Iye adzakhala pakati pa mabere anga+ usiku wonse. 14 Kwa ine, wachikondi wanga ali ngati duwa lofiirira+ m’minda ya mpesa ya ku Eni-gedi.”+
15 “Ndiwe wokongola kwabasi, wokondedwa wanga.+ Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa.”+
16 “Iwenso ndiwe wokongola,+ wachikondi wanga. Ndiwe mnyamata wosangalatsa kwambiri. Bedi+ lathunso ndi la masamba ofewa. 17 Nyumba yathu yokongola inamangidwa ndi mitengo ya mkungudza,+ ndipo kudenga* kwake kuli mitengo yofanana ndi mkungudza.