Nehemiya
12 Otsatirawa anali ansembe ndi Alevi amene anapita ndi Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa:+ Seraya, Yeremiya, Ezara, 2 Amariya,+ Maluki, Hatusi, 3 Sekaniya, Rehumu, Meremoti, 4 Ido, Ginetoi, Abiya, 5 Miyamini, Maadiya, Biliga, 6 Semaya,+ Yoyaribi, Yedaya,+ 7 Salelu,* Amoki,+ Hilikiya ndi Yedaya.+ Amenewa ndiwo anali atsogoleri a ansembe komanso a abale awo m’masiku a Yesuwa.+
8 Ndiyeno panali Alevi awa: Yesuwa,+ Binui,+ Kadimiyeli,+ Serebiya, Yuda ndi Mataniya.+ Mataniya ndi abale akewa anali oyang’anira oimba nyimbo zoyamika Mulungu. 9 Bakibukiya ndi Uni amene ndi abale awo, anaima moyang’anizana nawo kuti azigwira ntchito ya ulonda. 10 Yesuwa anabereka Yoyakimu,+ Yoyakimu anabereka Eliyasibu,+ Eliyasibu anabereka Yoyada.+ 11 Yoyada anabereka Yonatani, Yonatani anabereka Yaduwa.+
12 M’masiku a Yoyakimu kunali ansembe awa, atsogoleri a nyumba za makolo:+ woimira nyumba ya Seraya+ anali Meraya, woimira nyumba ya Yeremiya anali Hananiya. 13 Woimira nyumba ya Ezara+ anali Mesulamu, woimira nyumba ya Amariya anali Yehohanani. 14 Woimira nyumba ya Maluka anali Yonatani, woimira nyumba ya Sebaniya+ anali Yosefe. 15 Woimira nyumba ya Harimu+ anali Adena, woimira nyumba ya Merayoti anali Helikai. 16 Woimira nyumba ya Ido anali Zekariya, woimira nyumba ya Ginetoni anali Mesulamu. 17 Woimira nyumba ya Abiya+ anali Zikiri, woimira nyumba ya Miniyamini* anali . . . ,* woimira nyumba ya Moadiya anali Pilitai. 18 Woimira nyumba ya Biliga+ anali Samuwa, woimira nyumba ya Semaya anali Yehonatani. 19 Woimira nyumba ya Yoyaribi anali Matenai, woimira nyumba ya Yedaya+ anali Uzi. 20 Woimira nyumba ya Salai anali Kalai, woimira nyumba ya Amoki anali Ebere. 21 Woimira nyumba ya Hilikiya anali Hasabiya ndipo woimira nyumba ya Yedaya+ anali Netaneli.
22 M’masiku a Eliyasibu,+ Yoyada,+ Yohanani ndi Yaduwa,+ mayina a Alevi komanso ansembe anali kuwalemba m’gulu la atsogoleri a nyumba za makolo mpaka kudzafika m’nthawi ya ufumu wa Dariyo Mperisiya.
23 Mayina a ana aamuna a Levi, monga atsogoleri a nyumba za makolo,+ analembedwa m’buku la zochitika pa nthawi imeneyo mpaka kudzafika m’masiku a Yohanani, mwana wa Eliyasibu. 24 Atsogoleri a Alevi anali Hasabiya, Serebiya+ ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli.+ Ndipo abale awo anaima moyang’anizana nawo kuti azitamanda ndi kuyamika Mulungu mogwirizana ndi lamulo+ la Davide, munthu wa Mulungu woona. Gulu lililonse la alonda linaima moyandikana ndi gulu lina la alonda. 25 Mataniya,+ Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu+ anali kulondera monga alonda a m’zipata.+ Amenewa anali kulondera pafupi ndi zipinda zosungiramo zinthu m’zipata za kachisi. 26 Anthu amenewa anakhalapo m’masiku a Yoyakimu+ mwana wa Yesuwa+ amene anali mwana wa Yozadaki,+ komanso m’masiku a Nehemiya+ amene anali bwanamkubwa, ndi Ezara+ amene anali wansembe komanso wokopera Malemba.+
27 Ndiyeno mwambo wotsegulira+ mpanda wa Yerusalemu uli pafupi kuchitika, anthu anafunafuna Alevi m’malo awo onse ndi kubwera nawo ku Yerusalemu. Anachita izi kuti potsegulira mpandawo pakhale kusangalala ndi kuyamika+ Mulungu mwa kuimba nyimbo+ pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe+ ndi azeze.+ 28 Ana aamuna a oimbawo anasonkhana pamodzi kuchokera m’Chigawo*+ chapafupi, m’madera onse ozungulira Yerusalemu komanso m’midzi yonse kumene Anetofa anali kukhala.+ 29 Ena anachokera ku Beti-giligala+ komanso m’dera la Geba+ ndi la Azimaveti,+ pakuti kumeneko kunali midzi+ imene oimba anamanga kuzungulira Yerusalemu yense. 30 Ndiyeno ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ ndi kuyeretsanso anthu,+ zipata+ ndi khoma la mpandawo.+
31 Kenako ine ndinabwera ndi akalonga+ a Yuda pampandawo. Komanso ndinaika magulu akuluakulu awiri oimba nyimbo zoyamika+ Mulungu ndiponso magulu ena oti aziwatsatira pambuyo. Gulu limodzi la oimba linali kuyenda pampandawo kudzanja lamanja molunjika Chipata cha Milu ya Phulusa.+ 32 Hoshaya ndi hafu ya akalonga a Yuda anayamba kuyenda pambuyo pa oimbawo, 33 komanso Azariya, Ezara, Mesulamu, 34 Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya. 35 Mwa ana a ansembe oimba malipenga+ panalinso Zekariya mwana wa Yonatani. Yonatani anali mwana wa Semaya, Semaya anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali mwana wa Mikaya, Mikaya anali mwana wa Zakuri,+ ndipo Zakuri anali mwana wa Asafu.+ 36 Panalinso Semaya, Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, Yuda ndi Haneni, abale ake a Zekariya. Amenewa anali ndi zipangizo+ zoimbira za Davide, munthu wa Mulungu woona, ndipo Ezara+ wokopera Malemba ndiye anali kuwatsogolera. 37 Oimbawo atafika pa Chipata cha Kukasupe,+ gulu lowatsatira lija lili pambuyo pawo, anayenda pamalo okwera a mpandawo kudutsa pa Masitepe+ ochokera ku Mzinda wa Davide+ mpaka kukafika kumtunda kwa Nyumba ya Davide. Kenako anafika ku Chipata cha Kumadzi,+ kum’mawa kwa chipatacho.
38 Gulu lina loimba nyimbo zoyamika+ Mulungu linali kuyenda patsogolo, ndipo ine ndinali pambuyo pawo pamodzi ndi hafu ya anthuwo. Oimbawo anayenda pampandawo, kudutsa pamwamba pa Nsanja ya Mauvuni+ mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 39 Anadutsanso pamwamba pa Chipata cha Efuraimu,+ Chipata cha Mzinda Wakale,+ Chipata cha Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya+ ndi ku Chipata cha Nkhosa,+ ndipo anaima pa Chipata cha Alonda.
40 Kenako magulu awiri oimba nyimbo zoyamikawo+ anafika panyumba+ ya Mulungu woona. Ine pamodzi ndi atsogoleri amene ndinali nawo tinafikanso komweko.+ 41 Kunafikanso ansembe otsatirawa okhala ndi malipenga:+ Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, Hananiya, 42 Maaseya, Semaya, Eleazara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezeri. Ndipo oimba pamodzi ndi Izirahiya woyang’anira wawo anali kuimba mokweza.+
43 Pa tsiku limenelo anapereka nsembe zochuluka+ ndipo anasangalala+ pakuti Mulungu woona anawachititsa kusangalala kwambiri.+ Akazi+ ndi ana+ nawonso anasangalala, mwakuti phokoso la chisangalalo cha Yerusalemu linamveka kutali.+
44 Kuwonjezera apo, pa tsiku limenelo anaika amuna kuti aziyang’anira zipinda+ zosungiramo zinthu zosiyanasiyana,+ zopereka,+ mbewu zoyambirira+ ndi chakhumi.+ Anawapatsa udindo wosonkhanitsira m’zipindamo gawo loyenera kuperekedwa kwa ansembe ndi Alevi+ malinga ndi chilamulo,+ kuchokera m’minda yonse ya m’mizinda yawo. Yuda anali kusangalala chifukwa ansembe ndi Alevi+ anali kuchita utumiki wawo. 45 Choncho ansembe ndi Alevi pamodzi ndi oimba+ ndi alonda a pazipata+ anayamba kusamalira udindo+ wawo kwa Mulungu ndi kusunga lamulo lakuti azikhala oyera,+ malinga ndi lamulo la Davide ndi mwana wake Solomo. 46 Kalelo m’masiku a Davide ndi Asafu, kunali atsogoleri a oimba nyimbo+ ndipo anthu anali kuimba nyimbo zotamanda ndi kuyamika Mulungu.+ 47 Aisiraeli onse m’masiku a Zerubabele+ komanso m’masiku a Nehemiya+ anali kupereka gawo loyenera kwa oimba+ ndi alonda a pachipata+ malinga ndi zofunikira zawo za tsiku ndi tsiku. Ndipo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa Alevi.+ Aleviwo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa ana a Aroni.