2 Mbiri
28 Ahazi+ anali ndi zaka 20 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16.+ Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake.+ 2 Koma anayenda m’njira za mafumu a Isiraeli,+ ndipo anafika mpaka popangira Abaala+ zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula.+ 3 Ahazi anafukiza nsembe yautsi+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Iye anawotcha ana ake+ pamoto mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+ 4 Nthawi ndi nthawi ankapereka nsembe+ ndi kufukiza nsembe yautsi pamalo okwezeka,+ pamapiri,+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+
5 Choncho Yehova Mulungu wake anam’pereka m’manja+ mwa mfumu ya Siriya+ moti Asiriya anam’gonjetsa n’kugwira anthu ake ambiri kupita nawo ku Damasiko.+ Anam’perekanso m’manja mwa mfumu ya Isiraeli+ ndipo inam’gonjetsa n’kupha anthu ake ambirimbiri. 6 Chotero Peka+ mwana wa Remaliya+ anakapha anthu 120,000 ku Yuda tsiku limodzi. Onse amene anaphedwawo anali amuna olimba mtima. Iwo anaphedwa chifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo. 7 Kuwonjezera apo, Zikiri mwamuna wamphamvu wa fuko la Efuraimu,+ anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu mtsogoleri wa nyumba ya mfumu ndiponso Elikana yemwe anali wachiwiri kwa mfumu. 8 Komanso ana a Isiraeli anagwira abale awo okwana 200,000 n’kuwatenga. Pa anthu ogwidwawo panali amayi, ana aamuna ndi ana aakazi. Anafunkhanso zinthu zawo zambiri n’kupita nazo ku Samariya.+
9 Kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi. Iye anapita kukakumana ndi asilikali omwe anali kubwerera ku Samariya n’kuwauza kuti: “Tamverani! Yehova Mulungu wa makolo anu wapereka Ayuda m’manja mwanu chifukwa chakuti anawakwiyira kwambiri.+ N’chifukwa chake inuyo mwapha anthu pakati pawo mwaukali kwambiri,+ ndipo ukaliwo wafika mpaka kumwamba.+ 10 Tsopano mukufuna kusandutsa ana a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti akhale antchito anu aamuna+ ndi aakazi. Kodi inuyo mulibe milandu kwa Yehova Mulungu wanu? 11 Tsopano tamverani! Bwezani anthu amene mwawagwira kuchokera kwa abale anuwa,+ chifukwa mkwiyo wa Yehova wakuyakirani.”+
12 Kenako amuna ena omwe anali atsogoleri+ a ana a fuko la Efuraimu,+ anaukira asilikali amene anabwera kuchokera ku nkhondowo. Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu ndi Amasa mwana wa Hadilai. 13 Iwo anawauza kuti: “Musabweretse kuno anthu amene mwawagwirawo chifukwa tikhala ndi mlandu kwa Yehova. Mukufuna kuwonjezera machimo athu ndiponso mlandu wathu pakuti tili kale ndi mlandu waukulu,+ ndipo mkwiyo waukulu+ wa Mulungu wayakira Isiraeli.” 14 Choncho amuna onyamula zidawo+ anasiya anthuwo+ ndi zofunkha pamaso pa akalonga+ ndi pa mpingo wonse. 15 Kenako amuna amene anachita kusankhidwa powatchula mayina+ ananyamuka n’kutenga anthu ogwidwawo. Anthu onse amene sanavale* zovala anawaveka zovala+ zimene anafunkha ndipo anawavekanso nsapato. Anawapatsa chakudya+ ndi zakumwa,+ ndipo anawadzoza mafuta. Kuwonjezera apo, aliyense amene anali kuyenda movutikira anamukweza+ pabulu. Atatero anatenga anthuwo n’kupita nawo ku Yeriko,+ kumzinda wa mitengo ya kanjedza,+ kufupi ndi abale awo. Pambuyo pake iwo anabwerera ku Samariya.+
16 Pa nthawi imeneyo, Mfumu Ahazi+ inatumiza uthenga kwa mafumu a Asuri+ kuti adzam’thandize. 17 Aedomu+ anabweranso n’kudzapha Ayuda, ndipo anagwira anthu ena n’kuwatenga. 18 Nawonso Afilisiti+ anaukira mizinda ya Yuda ya ku Sefela+ ndi ku Negebu+ n’kulanda mizinda ya Beti-semesi,+ Aijaloni,+ Gederoti,+ Soko+ ndi midzi yake yozungulira, Timuna+ ndi midzi yake yozungulira, komanso Gimizo ndi midzi yake yozungulira, n’kuyamba kukhala kumeneko. 19 Zinatero chifukwa chakuti Yehova anatsitsa+ Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Isiraeli, popeza analekerera kuti makhalidwe oipa achuluke mu Yuda.+ Iye anachita zinthu zambiri zosakhulupirika kwa Yehova.
20 M’kupita kwa nthawi, Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri anabwera kudzamenyana naye. Iye anam’sautsa+ ndipo sanam’limbikitse. 21 Ahazi anatenga zinthu za m’nyumba ya Yehova,+ za m’nyumba ya mfumu+ ndi za m’nyumba za akalonga,+ n’kuzipereka kwa mfumu ya Asuri+ monga mphatso, koma zimenezi sizinam’thandize. 22 Pa nthawi imene Mfumu Ahazi inali kusautsidwa, inawonjezera kuchita zosakhulupirika kwa Yehova.+ 23 Ahaziyo anayamba kupereka nsembe kwa milungu+ ya ku Damasiko+ imene inali kumuukira, ndipo anati: “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a Siriya ikuwathandiza,+ ndipereka nsembe kwa iyo kuti inenso indithandize.”+ Koma milunguyo inakhala chopunthwitsa kwa iye ndi kwa Aisiraeli onse.+ 24 Kuwonjezera apo, Ahazi anasonkhanitsa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona+ n’kuziphwanyaphwanya. Komanso anatseka zitseko+ za nyumba ya Yehova. Kenako anakadzimangira maguwa ansembe m’makona onse a mu Yerusalemu.+ 25 M’mizinda yonse ya Yuda anamangamo malo okwezeka+ operekera nsembe zautsi kwa milungu ina.+ Chotero anakwiyitsa+ Yehova Mulungu wa makolo ake.
26 Nkhani zina+ zokhudza Ahazi, zoyambirira ndi zomalizira, ndiponso njira zake zonse, zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli. 27 Pomalizira pake, Ahazi anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anaikidwa m’manda mumzinda, ku Yerusalemu. Iye sanaikidwe m’manda a mafumu a Isiraeli.+ Kenako Hezekiya mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.