Kwa Agalatiya
1 Ine Paulo,+ ndine mtumwi,+ osati wochokera kwa anthu kapena woikidwa kudzera mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu+ ndi mwa Mulungu Atate+ amene anamuukitsa kwa akufa.+ 2 Ineyo, pamodzi ndi abale onse amene ali ndi ine,+ ndikulembera kalata mipingo ya ku Galatiya:+
3 Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+ 4 Iye anadzipereka chifukwa cha machimo athu,+ kuti atilanditse ku nthawi* yoipayi,+ mogwirizana ndi chifuniro+ cha Mulungu ndi Atate wathu. 5 Ulemu ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya.+ Ame.
6 Ndine wodabwa kuti mwapatutsidwa mwamsanga, kuchoka kwa Iye+ amene anakuitanani mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Khristu,+ ndipo mwakopeka ndi uthenga wabwino wamtundu wina.+ 7 Koma umenewo sikuti ndi uthenganso wabwino, kungoti pali anthu ena amene akukusokonezani+ ndipo akufuna kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu.+ 8 Komabe, ngati ifeyo kapena mngelo wochokera kumwamba angalengeze nkhani ina kwa inu monga uthenga wabwino, koma nkhaniyo n’kukhala yosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembereredwa.+ 9 Monga mmene tanenera kale, ndikunenanso kuti, Aliyense amene akulengeza nkhani ina kwa inu monga uthenga wabwino, koma yosiyana ndi imene munalandira,+ ameneyo akhale wotembereredwa.
10 Kodi ndiye kuti tsopano ndikufuna kukopa anthu kapena Mulungu? Kapena kodi ndikungofuna kukondweretsa anthu?+ Ndikanakhala kuti ndikukondweretsabe anthu,+ sindikanakhala kapolo wa Khristu.+ 11 Pakuti ndikufuna mudziwe, abale, kuti uthenga wabwino umene ndinaulengeza monga uthenga wabwino sunachokere kwa anthu.+ 12 Uthengawu sindinaulandire kwa munthu, ndipo sindinachite kuuphunzira mwanjira ina, koma Yesu Khristu ndiye amene anandiululira uthenga umenewu.+
13 Munamva ndithu zimene ndinali kuchita ndili m’Chiyuda,+ kuti ndinkazunza kwambiri+ mpingo wa Mulungu ndi kupitirizabe kuuwononga.+ 14 Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga.+ Pakuti ndinali wodzipereka kwambiri+ pa miyambo+ ya makolo anga. 15 Koma pamene Mulungu, amene anandichititsa kuti ndibadwe, anandiitana+ mwa kukoma mtima kwake kwakukulu,+ kunamukomera 16 kuulula za Mwana wake kudzera mwa ine,+ kuti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina uthenga wabwino wonena za iye.+ Sindinapite kukakambirana ndi anthu a thupi la nyama ndi magazi nthawi yomweyo.+ 17 Sindinapitenso ngakhale ku Yerusalemu kwa amene anakhala atumwi ndisanakhale ine,+ koma ndinapita ku Arabiya, kenako ndinabwereranso ku Damasiko.+
18 Ndiye pambuyo pa zaka zitatu ndinapita ku Yerusalemu+ kukacheza kwa Kefa+ ndipo ndinakhala naye masiku 15. 19 Koma sindinaone mtumwi winanso kupatulapo Yakobo,+ m’bale+ wa Ambuye. 20 Zimene ndikukulemberanizi, ndikukuuzani pamaso pa Mulungu kuti sindikunama.+
21 Kenako ndinalowa+ m’madera a Siriya ndi Kilikiya. 22 Koma nkhope yanga inali yosadziwika kumipingo yogwirizana ndi Khristu, ya ku Yudeya.+ 23 Iwo ankangomva kuti: “Munthu amene anali kutizunza kale uja,+ tsopano akulengeza uthenga wabwino wonena za chikhulupiriro chimene anali kuwononga.”+ 24 Choncho anthuwo anayamba kulemekeza+ Mulungu chifukwa cha ine.
2 Ndiyeno patapita zaka 14, ndinapita ku Yerusalemu kachiwiri+ limodzi ndi Baranaba,+ ndipo ndinatenganso Tito. 2 Ndinapita kumeneko chifukwa ndinauzidwa m’masomphenya kuti ndipiteko.+ Ndipo ndinafotokozera+ amuna odalirika, uthenga wabwino umene ndikuulalikira kwa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezo chifukwa ndinkaopa kuti mwina ndinali kuthamanga+ popanda phindu, kapena ndinali nditathamanga kale pachabe.+ Koma ndinawafotokozera zimenezi kumbali. 3 Ndipo ngakhale Tito,+ amene ndinali naye limodzi, sanafunikire kudulidwa,+ ngakhale kuti iye ndi Mgiriki. 4 Chifukwa cha abale onyenga+ amene analowa pakati pathu mwakachetechete+ ndiponso mozemba monga akazitape, n’cholinga choti awononge ufulu wathu+ umene tili nawo mogwirizana ndi Khristu Yesu, ndiponso kuti atisandutse akapolo+ . . . 5 anthu amenewa sitinawagonjere,+ ngakhale kwa ola limodzi, kuti inuyo mupitirize kukhala ndi choonadi+ cha uthenga wabwino.
6 Tsopano kunena za anthu amene ankaoneka ngati apadera,+ kaya pa chiyambi anali anthu otani, zilibe kanthu kwa ine,+ Mulungu sayang’ana nkhope ya munthu,+ kwa ine, amuna odalirika amenewo sanandiphunzitse kalikonse katsopano. 7 Koma iwo ataona kuti ndapatsidwa+ ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu osadulidwa,+ mmene Petulo anapatsidwira ntchito yoti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu odulidwa,+ 8 (pajatu iye amene anapatsa Petulo mphamvu yokhala mtumwi kwa anthu odulidwa ndi amene anapatsanso ine mphamvu+ kuti ndikalalikire kwa anthu a mitundu ina) 9 iwo atazindikira kukoma mtima kwakukulu+ kumene ndinapatsidwa,+ Yakobo,+ Kefa ndi Yohane, amene anali ngati mizati,+ anagwira chanza ineyo ndi Baranaba.+ Anatero posonyeza kuti agwirizana nazo+ zoti ife tipite kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo apite kwa odulidwa. 10 Anangotipempha kuti tizikumbukira aumphawi.+ Ndipo ndayesetsa moona mtima kuchita zimenezi.+
11 Koma Kefa+ atabwera ku Antiokeya,+ ndinamutsutsa pamasom’pamaso, chifukwa anali wolakwa.+ 12 Pakuti asanafike anthu ena ochokera kwa Yakobo,+ iye anali kudya+ limodzi ndi anthu a mitundu ina, koma anthuwo atafika, iye anadzipatula ndipo anasiya kuchitira nawo zinthu limodzi, chifukwa ankaopa+ anthu odulidwawo.+ 13 Ayuda enawonso anagwirizana naye pochita zachiphamaso zimenezi.+ Ngakhale Baranaba+ nayenso anachita nawo zachiphamasozi. 14 Koma nditaona kuti sanali kuyenda mogwirizana ndi choonadi cha uthenga wabwino,+ ndinanena kwa Kefa pamaso pa onse+ kuti: “Ngati iweyo, ngakhale kuti ndiwe Myuda, ukukhala ngati anthu a mitundu ina, osati ngati Ayuda, n’chifukwa chiyani ukufuna kuchititsa anthu a mitundu ina kuti azitsatira chikhalidwe cha Ayuda?”+
15 Ifeyo ndife a mtundu wachiyuda.+ Si ife ochimwa+ ochokera mwa anthu a mitundu ina. 16 Popeza tikudziwa kuti munthu amayesedwa wolungama+ mwa kukhulupirira+ Khristu Yesu, osati chifukwa cha ntchito za chilamulo, ife takhulupirira Khristu Yesu. Tachita zimenezi kuti tiyesedwe olungama chifukwa cha chikhulupiriro chathu mwa Khristu,+ osati mwa ntchito zotsatira chilamulo. Tatero chifukwa palibe munthu adzayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito zotsatira chilamulo.+ 17 Tsopano ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama kudzera mwa Khristu,+ tapezedwanso kuti ndife ochimwa,+ kodi ndiye kuti Khristu wakhala mtumiki wa uchimo?+ Ayi ndithu. 18 Pakuti ngati ndikumanganso zomwezo zimene ndinagwetsa,+ ndiye kuti ndikusonyeza kuti ndine wophwanya malamulo.+ 19 Mwa chilamulo, ine ndinafa ku chilamulo,+ moti sindingachitsatirenso, kuti ndikhale wamoyo kwa Mulungu.+ 20 Ndinapachikidwa limodzi ndi Khristu.+ Si inenso amene ndikukhala ndi moyo,+ koma Khristu ndi amene akukhala ndi moyo mwa ine.+ Zoonadi, moyo umene ndikukhala tsopano,+ ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.+ 21 Sindikukankhira kumbali kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ chifukwa ngati munthu amakhala wolungama kudzera mwa chilamulo,+ ndiye kuti Khristu anangofa pachabe.+
3 Kalanga ine, Agalatiya opusa inu! Kodi ndani anakupotozani maganizo,+ inu amene munakhala ngati mwaona Yesu Khristu atapachikidwa pamtengo?+ 2 Ndikufuna mundiuze: Kodi munalandira mzimu+ chifukwa cha ntchito za chilamulo+ kapena chifukwa chokhulupirira zimene munamva?+ 3 Kodi ndinu opusa chonchi? Munayamba ndi kudalira mzimu,+ kodi tsopano mukufuna kumaliza ndi kudalira zinthu zochokera kwa anthu opanda ungwiro?+ 4 Kodi kuvutika konse kuja kunangopita pachabe?+ Ndikukhulupirira kuti sikunapite pachabe. 5 Iye amene amakupatsani mzimu+ ndi kuchita zinthu zamphamvu+ pakati panu, kodi amazichita chifukwa chakuti inuyo mukuchita ntchito za chilamulo kapena chifukwa chakuti munakhulupirira uthenga wabwino umene munamva? 6 Zili monga mmene Abulahamu “anakhulupirira mwa Yehova, ndipo Mulunguyo anamuona Abulahamu ngati wolungama.”+
7 Ndithudi mukudziwa kuti amene amakhalabe ndi chikhulupiriro+ ndiwo ana a Abulahamu.+ 8 Ndiyeno, Malemba ataoneratu kuti Mulungu adzayesa anthu a mitundu ina kukhala olungama chifukwa cha chikhulupiriro, analengezeratu uthenga wabwino kwa Abulahamu, kuti: “Kudzera mwa iwe, mitundu yonse idzadalitsidwa.”+ 9 Chotero, amene akugwiritsitsa chikhulupiriro akudalitsidwa+ limodzi ndi Abulahamu wokhulupirikayo.+
10 Pakuti onse odalira ntchito za chilamulo ndi otembereredwa, chifukwa Malemba amati: “Ndi wotembereredwa aliyense wosapitiriza kuyenda m’zinthu zonse zolembedwa mumpukutu wa Chilamulo ndi kuzichita.”+ 11 Komanso, mfundo yakuti palibe munthu amene angaonedwe ngati wolungama+ ndi Mulungu mwa chilamulo ndi yoonekeratu, chifukwa “wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.”+ 12 Tsopano, Chilamulo sichidalira chikhulupiriro, koma “wochita za m’Chilamulo adzakhala ndi moyo potsatira chilamulocho.”+ 13 Khristu anatigula+ ndi kutimasula+ ku temberero la Chilamulo ndipo iyeyo anakhala temberero+ m’malo mwa ife, chifukwa Malemba amati: “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.”+ 14 Cholinga chake chinali chakuti mitundu ipeze madalitso amene Abulahamu analonjezedwa kudzera mwa Yesu Khristu,+ kuti tidzalandire mzimu wolonjezedwawo+ chifukwa cha chikhulupiriro chathu.+
15 Abale, ndipereke fanizo mogwirizana ndi zimene zimachitika pakati pa anthu: Pangano likakhazikitsidwa, ngakhale kuti ndi pangano la anthu, palibe angachotsepo kapena kuwonjezerapo mfundo zina.+ 16 Tsopano, malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu+ ndi kwa mbewu yake.+ Malemba sanena kuti: “Kwa mbewu zako,” ngati kuti mbewuzo n’zambiri, koma amanena za mbewu imodzi+ kuti: “Kwa mbewu yako,”+ amene ndi Khristu.+ 17 Komanso ineyo ndikuti: Chilamulo chimene chinadzakhalapo zaka 430+ pambuyo pa panganolo, limene kalekalelo linatsimikizidwa ndi Mulungu,+ sichingathetse mphamvu ya panganolo, kapena kufafaniza lonjezolo.+ 18 Pakuti ngati cholowa chimene Mulungu amapereka chimadzera m’chilamulo, ndiye kuti sichidaliranso lonjezo,+ koma Mulungu mokoma mtima wachipereka kwa Abulahamu mwa lonjezo.+
19 Nanga tsopano Chilamulo chinakhalapo chifukwa chiyani? Anachiwonjezerapo kuti machimo aonekere,+ mpaka amene ali mbewuyo atafika,+ amene anapatsidwa lonjezolo. Ndipo Chilamulocho chinaperekedwa kudzera mwa angelo,+ kudzeranso m’dzanja la mkhalapakati.+ 20 Tsopano, sipakhala mkhalapakati ngati pangano lili la munthu mmodzi yekha, koma Mulungu anali yekha.+ 21 Chotero kodi Chilamulo chimatsutsa malonjezo a Mulungu?+ Zimenezo sizingachitike ngakhale pang’ono. Pakanaperekedwa lamulo lopatsa moyo,+ bwenzi chilungamo chikudzera m’chilamulo.+ 22 Koma Malemba+ anatsekera zinthu zonse n’kuziika pansi pa uchimo,+ kuti lonjezolo, limene limakhalapo mwa kukhulupirira Yesu Khristu, liperekedwe kwa okhulupirirawo.+
23 Komabe chikhulupirirocho chisanafike,+ chilamulo chinali kutiyang’anira+ ndipo chinatiika mu ukapolo. Pa nthawi imeneyo, tinali tikuyembekezera chikhulupiriro chimene chinali kudzaonekera.+ 24 N’chifukwa chake Chilamulo chakhala mtsogoleri* wotifikitsa kwa Khristu,+ kuti tiyesedwe olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro. 25 Koma popeza chikhulupirirocho tsopano chafika,+ sitilinso pansi pa mtsogoleriyo.+
26 Koma nonsenu ndinu ana+ a Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu. 27 Pakuti nonsenu amene munabatizidwa mwa Khristu+ mwavala Khristu.+ 28 Palibe Myuda kapena Mgiriki,+ palibe kapolo kapena mfulu,+ palibenso mwamuna kapena mkazi.+ Nonsenu ndinu munthu mmodzi mwa Khristu Yesu.+ 29 Ndiponso ngati muli a Khristu, ndinudi mbewu ya Abulahamu,+ olandira cholowa mogwirizana ndi lonjezolo.+
4 Tsopano ndikuuzeni kuti, wolandira cholowa akakhala kamwana, iye sasiyana konse ndi kapolo,+ ngakhale ali mwini zinthu zonse. 2 Amakhalabe pansi pa amuna oyang’anira ana+ ndiponso anthu oyang’anira zinthu za mbuye wawo, kufikira tsiku limene bambo ake anaikiratu. 3 N’chimodzimodzinso ifeyo. Pamene tinali tiana, tinali akapolo a mfundo zachibwanabwana+ zimene anthu a m’dzikoli amayendera. 4 Koma nthawi itakwana,+ Mulungu anatumiza Mwana wake,+ amene anadzabadwa kwa mkazi+ ndipo anadzakhala pansi pa chilamulo.+ 5 Zinatero kuti amasule anthu okhala pansi pa chilamulo mwa kuwagula,+ kutinso Mulungu atitenge ife kukhala ana ake.+
6 Tsopano pakuti ndinu ana ake, Mulunguyo watitumizira mzimu+ wa Mwana wake m’mitima yathu ndipo mzimuwo ukufuula kuti: “Abba,* Atate!”+ 7 Chotero si iwenso kapolo, koma mwana ndipo ngati uli mwana, ndiwenso wolandira cholowa kudzera mwa Mulungu.+
8 Ngakhale zili choncho, pamene munali osadziwa Mulungu,+ munali akapolo a zinthu zimene mwachilengedwe si milungu.+ 9 Koma tsopano pamene mwadziwa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano pamene mwadziwidwa ndi Mulungu,+ mukubwereranso bwanji ku mfundo zachibwanabwana,+ zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake,+ n’kumafuna kukhalanso akapolo ake?+ 10 Mukusunga mwakhama masiku,+ miyezi,+ nyengo ndi zaka. 11 Ndikuda nkhawa, kuti mwina ntchito imene ndaigwira pa inu ipita pachabe.+
12 Ndikukupemphani abale anga, khalani monga ine+ chifukwa inenso ndinali ngati inuyo kale.+ Simunandilakwire ayi.+ 13 Koma mukudziwa kuti nthawi yoyamba imene ndinalengeza uthenga wabwino kwa inu chifukwa chakuti ndinali kudwala,+ 14 inuyo simunanyansidwe ndi matenda anga, amene anali mayesero kwa inu, ndipo simunalavule malovu ponyansidwa nawo, koma munandilandira ngati mngelo+ wa Mulungu, ngati Khristu Yesu.+ 15 Chili kuti nanga chimwemwe chimene munali nacho poyamba chija?+ Pakuti ndikunenetsa kuti, zikanakhala zotheka, mukanakolowola maso anu n’kundipatsa.+ 16 Kodi ndakhala mdani+ wanu tsopano chifukwa ndakuuzani zoona?+ 17 Anthu ena akuyesetsa kwambiri kuti akukopereni kwa iwowo,+ osati ndi zolinga zabwino, koma kuti akutsekerezeni kuti musabwere kwa ine, kuti inuyo muyesetse kuwatsatira.+ 18 Ngati munthu akukufunani kwambiri pa chifukwa chabwino, n’zabwino kwa inu.+ Zimenezi zikachitika osati pa nthawi imene ine ndili nanu limodzi yokha,+ komanso nthawi zonse, 19 ndiye kuti n’zabwino kwa inu ana anga.+ Ine ndayambanso kumva zopweteka zimene ndinamva pokuberekani, mpaka Khristu adzakhazikike mwa inu.+ 20 Panopa ndikanakonda kukhala pakati panu+ kuti ndilankhule mosiyanako, chifukwa mwandithetsa nzeru.+
21 Tandiuzani, inu amene mukufuna kutsatira chilamulo,+ Kodi simukumva zimene Chilamulocho chikunena?+ 22 Mwachitsanzo, Malemba amati Abulahamu anabereka ana aamuna awiri, wina kwa mdzakazi*+ ndipo wina kwa mkazi amene anali mfulu.+ 23 Koma mwana amene anabadwa kwa mdzakazi uja anabadwa monga mmene ana onse amabadwira,+ pamene mwana winayo amene anabadwa kwa mkazi amene anali mfulu anabadwa mwa lonjezo.+ 24 Zinthu zimenezi zili ndi tanthauzo lophiphiritsira,+ pakuti azimayi amenewa akuimira mapangano awiri.+ Loyamba ndi pangano la paphiri la Sinai,+ limene limabereka ana oti akhale akapolo. Pangano limenelo ndiye Hagara uja. 25 Tsopano, Hagara ameneyu akutanthauza Sinai,+ phiri la ku Arabiya, ndipo masiku ano akufanana ndi Yerusalemu, pakuti ali mu ukapolo+ pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu+ wam’mwamba ndi mfulu, ndipo ndiye mayi wathu.+
27 Pakuti Malemba amati: “Kondwera, mkazi wosabereka iwe amene sunaberekepo mwana. Kuwa ndipo fuula mokondwa, iwe mkazi amene sunamvepo zowawa za pobereka, pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.”+ 28 Tsopano ifeyo abale, ndife ana a lonjezo monga mmene analili Isaki.+ 29 Koma monga mmene zinalili pa nthawiyo, kuti wobadwa monga mmene ana onse amabadwira anayamba kuzunza+ wobadwa mwa mzimu, ndi mmenenso zilili masiku ano.+ 30 Ngakhale zili choncho, kodi Malemba amati chiyani? “Thamangitsani mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, pakuti sizingatheke mwana wa mdzakazi kudzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wa mkazi waufulu.”+ 31 Chotero abale, ife ndife ana a mkazi waufulu,+ osati a mdzakazi.+
5 Khristu anatimasula kuti tikhale ndi ufulu umenewu.+ Chotero khalani olimba,+ ndipo musalole kumangidwanso m’goli laukapolo.+
2 Tamverani! Ine Paulo, ndikukuuzani kuti mukadulidwa,+ Khristu sadzakhala waphindu kwa inu. 3 Kuwonjezera apo, ndikunenetsa kwa munthu aliyense amene akudulidwa, kuti afunikanso kuchita zonse za m’Chilamulo.+ 4 Inuyo amene mukufuna kuyesedwa olungama mwa chilamulo, mwadzilekanitsa ndi Khristu,+ kaya mukhale ndani, mwagwera kunja kwa kukoma mtima kwake kwakukulu.+ 5 Koma kudzera mwa mzimu, ife tikuyembekezera mwachidwi chilungamo cholonjezedwacho, chimene chimadza mwa chikhulupiriro.+ 6 Pakuti kwa Khristu Yesu, kudulidwa kapena kusadulidwa zilibe phindu,+ koma chikhulupiriro+ chimene chimagwira ntchito kudzera m’chikondi.+
7 Munali kuthamanga bwino.+ Anakusokonezani ndani kuti musapitirize kumvera choonadi?+ 8 Kukopeka kumeneku sikunachokere kwa Iye amene anakuitanani.+ 9 Chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa mtanda wonse.+ 10 Ndikukhulupirira+ kuti inu amene muli ogwirizana+ ndi Ambuye, simudzasintha maganizo, koma munthu amene amakuvutitsani,+ adzaweruzidwa+ kaya akhale ndani. 11 Kunena za ine abale, ngati ndimalalikirabe kuti anthu azidulidwa, n’chifukwa chiyani ndikuzunzidwabe? Ndithudi, mtengo wozunzikirapo,+ womwe ndi chopunthwitsa,+ ukanakhala utachotsedwa.+ 12 Ndikanakonda kuti anthu amene akufuna kukupotozani maganizo,+ afulidwe.+
13 Zoonadi abale, munaitanidwa kuti mukhale aufulu,+ musayese ngakhale pang’ono kugwiritsa ntchito ufulu umenewu polimbikitsira zilakolako za thupi,+ koma tumikiranani mwachikondi.+ 14 Pakuti Chilamulo chonse chimakwaniritsidwa+ m’mawu akuti: “Uzikonda mnzako ngati mmene umadzikondera wekha.”+ 15 Koma mukamalumana ndi kudyana nokhanokha,+ chenjerani kuti mungawonongane.+
16 M’malomwake ndikuti, Pitirizani kuyenda mwa mzimu,+ ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.+ 17 Pakuti zilakolako za thupi zimalimbana ndi mzimu,+ mzimunso umalimbana ndi thupi. Zinthu ziwiri zimenezi zimatsutsana, choncho zinthu zimene mumafuna kuchita simuzichita.+ 18 Komanso ngati mukutsogoleredwa ndi mzimu,+ simuli pansi pa chilamulo.+
19 Tsopano, ntchito za thupi zimaonekera.+ Ntchitozi ndizo dama,*+ zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira,+ 20 kupembedza mafano, kuchita zamizimu,+ udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, 21 kaduka, kumwa mwauchidakwa,*+ maphwando aphokoso, ndi zina zotero. Ponena za zinthu zimenezi, ndikukuchenjezeranitu, ngati mmene ndinachitira poyamba paja, kuti anthu amene amachita zimenezi+ sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.+
22 Koma makhalidwe* amene mzimu woyera umatulutsa+ ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino,+ chikhulupiriro, 23 kufatsa ndi kudziletsa.+ Palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.+ 24 Ndiponso anthu amene ali a Khristu Yesu, anapachika thupi lawo pamodzi ndi zikhumbo zake ndi zilakolako zake.+
25 Ngati tikukhala mwa mzimu, tiyeninso tipitirize kuyenda motsogoleredwa ndi mzimuwo.+ 26 Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano+ pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.+
6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika+ mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu,+ yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale,+ kuopera kuti iyenso angayesedwe.+ 2 Musaleke kunyamulirana zolemetsa.+ Mukatero mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.+ 3 Pakuti ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero,+ akudzinyenga. 4 Koma aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani.+ Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera+ ndi munthu wina. 5 Pakuti aliyense ayenera kunyamula katundu wake.+
6 Komanso, aliyense amene akuphunzitsidwa mawuwo+ agawane+ zinthu zonse zabwino ndi amene akumuphunzitsayo.+
7 Musanyengedwe,+ Mulungu sapusitsika.+ Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+ 8 Pakuti amene akufesa ndi cholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera m’thupi lakelo,+ koma amene akutsatira mzimu wa Mulungu+ adzakolola moyo wosatha kuchokera ku mzimuwo.+ 9 Choncho tisaleke kuchita zabwino,+ pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.+ 10 Chotero ngati tingathe,+ tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.+
11 Taonani zilembo zikuluzikulu zimene ndakulemberani ndekha ndi dzanja langali.+
12 Onse ofuna kudzionetsa ngati abwino pamaso pa anthu ndi amene akukuumirizani kuti muzidulidwa.+ Akuchita zimenezi kuti asazunzidwe chifukwa cha mtengo wozunzikirapo wa Khristu,+ amene ndi Yesu. 13 Pakuti ngakhale amene akudulidwawo sasunga Chilamulo,+ koma akufuna inuyo mudulidwe kuti iwo azidzitama chifukwa cha zimene zachitika pathupi lanu. 14 Ineyo sindidzadzitama pa chifukwa china chilichonse, koma chifukwa cha mtengo wozunzikirapo+ wa Ambuye wathu Yesu Khristu basi. Kudzera mwa ameneyu, kwa ine dziko lapansi lapachikidwa, ndipo malinga ndi kuona kwa dziko lapansi,+ ineyo ndapachikidwa. 15 Pakuti kudulidwa kapena kusadulidwa si kanthu,+ koma chofunika ndi kukhala wolengedwa mwatsopano.+ 16 Ndipo onse otsatira lamulo limeneli la mmene tiyenera kukhalira, amene ndi Isiraeli wa Mulungu, akhale ndi mtendere ndiponso chifundo.+
17 Kuyambira tsopano, pasapezeke munthu wondivutitsa, pakuti thupi langali lili ndi zipsera za chizindikiro+ cha kapolo wa Yesu.+
18 Abale, kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kukhale nanu chifukwa cha mzimu+ umene mumausonyeza. Ame.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “mtsogoleri” amatanthauza munthu amene anali kugwira ntchito yoyang’anira kapena kuteteza ana.
“Abba” ndi mawu achiaramu otanthauza “ababa,” kapena, “Inu bambo anga!”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 7.
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa n’cholinga chofuna kuledzera.
Mawu ake enieni, “chipatso.”