Yobu
13 “Tamverani! Zonsezi maso anga aziona,
Ndipo khutu langa lamva ndi kuziganizira.
7 Kodi amuna inu mulankhula zopanda chilungamo m’malo mwa Mulungu?
Mulankhula zachinyengo m’malo mwa iye?+
9 Kodi zingakhale bwino kuti iye akufufuzeni?+
Kapena mungam’pusitse ngati mmene mungapusitsire munthu?
10 Iye adzakudzudzulani ndithu,+
Mukadzayesera kuchita zinthu zokondera mwakabisira.+
11 Kodi kulemekezeka kwake sikudzakuchititsani mantha?
Kodi iye sadzakuchititsani kuti muope?+
12 Mawu anu osaiwalika ndiwo miyambi yopanda pake ngati phulusa.
Mayankho anu odziteteza ali ngati zishango zadothi.+
13 Khalani chete pamaso panga, kuti ineyo ndilankhule.
Kenako chilichonse chondifikira chindifikire.
15 Ngati iye atandipha, kodi sindidzadikirira?+
Komabe ndingatsutsane naye pamasom’pamaso za njira zanga.
20 Pali zinthu ziwiri zokha zoti musandichitire.
Mukatero sindidzabisala pamaso panu.+
21 Ikani dzanja lanu kutali ndi ine,
Ndipo kuopsa kwanu kusandichititse mantha.+
22 Muitane kuti ine ndivomere.
Kapena ndilankhule ndipo inu mundiyankhe.
23 Kodi ine ndinalakwa ndiponso kuchimwa mwa njira yanji?
Ndidziwitseni kulakwa kwanga ndiponso tchimo langa.
25 Kodi mukuopseza ine tsamba lachabechabe louluzika ndi mphepo?
Kapena mukuthamangitsa ine udzu wouma wachabechabe?
26 Pakuti inu mukupitiriza kundilembera zinthu zowawa,+
Ndipo mukundipatsa zotsatira za zolakwa zimene ndinachita ndili mnyamata.+