Yakobo
1 Ine Yakobo,+ kapolo+ wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, ndikupereka moni kwa mafuko 12+ amene ali obalalika:+
2 Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana,+ 3 monga mukudziwira kuti chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira.+ 4 Koma mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira+ ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.+
5 Choncho ngati wina akusowa nzeru,+ azipempha kwa Mulungu,+ ndipo adzamupatsa,+ popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.+ 6 Koma azipempha+ ndi chikhulupiriro, osakayikira m’pang’ono pomwe,+ pakuti wokayikira ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo+ ndi lowindukawinduka. 7 Munthu wotero asaganize kuti adzalandira kanthu kwa Yehova,+ 8 chifukwa choti iye ndi wokayikakayika,+ wosakhazikika+ m’njira zake zonse.
9 Koma m’bale wonyozeka akondwere chifukwa tsopano wakwezedwa,+ 10 ndipo wachuma+ akondwere chifukwa tsopano watsitsidwa, chifukwa mofanana ndi duwa la zomera, wachumayo adzafota.+ 11 Dzuwa limatuluka ndi kutentha kwake n’kufotetsa zomera, ndipo maluwa a zomerazo amathothoka. Kukongola kwake kumatha. Momwemonso munthu wachuma adzafa akutsatira njira ya moyo wake.+
12 Wodala ndi munthu wopirira mayesero,+ chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto* ya moyo,+ umene Yehova analonjeza onse omukonda.+ 13 Munthu akakhala pa mayesero+ asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa. 14 Koma munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.+ 15 Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.+ Nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.+
16 Abale anga okondedwa, musasocheretsedwe.+ 17 Mphatso iliyonse yabwino+ ndi yangwiro imachokera kumwamba,+ pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo,+ ndipo iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.+ 18 Pakuti mwa chifuniro+ chake, iye anatibala ife ndi mawu a choonadi.+ Anachita zimenezi kuti tikhale zipatso zoyambirira+ pa zolengedwa zake.
19 Abale anga okondedwa, dziwani izi: Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula,+ wosafulumira kukwiya,+ 20 chifukwa mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.+ 21 Choncho siyani khalidwe lililonse lonyansa ndiponso siyani khalidwe lochita zoipa, lomwe ndi losafunika,+ ndipo vomerezani mofatsa mawu okhoza kupulumutsa miyoyo yanu,+ kuti abzalidwe mwa inu.+
22 Komabe muzichita zimene mawu amanena,+ osati kungomva chabe, n’kumadzinyenga ndi maganizo onama.+ 23 Pakuti ngati munthu ali wongomva mawu, koma wosachita,+ ali ngati munthu wodziyang’anira nkhope yake pagalasi. 24 Iye amadziyang’ana koma akachokapo, nthawi yomweyo amaiwala kuti ndi munthu wotani. 25 Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala+ polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.+
26 Ngati munthu akudziona ngati wopembedza,+ koma salamulira lilime lake,+ ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake,+ kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.+ 27 Kupembedza koyera+ ndi kosaipitsidwa+ kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye+ ndi akazi amasiye+ m’masautso awo,+ ndi kukhala wopanda banga+ la dzikoli.+
2 Abale anga, kodi mukuganiza kuti mukukhulupirira Ambuye wathu Yesu Khristu, amene ali ulemerero+ wathu, pamene mukuchita zokondera?+ 2 Pakuti munthu wovala mphete zagolide ndi zovala zapamwamba akafika pamsonkhano+ wanu, ndipo winanso wosauka wovala zovala zonyansa akafika,+ 3 inu mumasangalala ndi wovala zapamwamba uja+ ndipo mumamuuza kuti: “Khalani pamalo pabwinopa,” koma kwa wosauka uja mumati: “Imirira choncho,” kapena: “Khala pansipa pafupi ndi chopondapo mapazi anga.” 4 Mumasankhana pakati panu+ ndipo mwakhala oweruza+ opereka zigamulo zoipa,+ si choncho kodi?
5 Tamverani abale anga okondedwa. Mulungu anasankha anthu amene ali osauka+ m’dzikoli kuti akhale olemera+ m’chikhulupiriro ndi olandira cholowa cha ufumu umene anaulonjeza kwa omukonda,+ sanatero kodi? 6 Koma inu simulemekeza munthu wosauka. Kodi si olemera amene amakusautsani+ ndi kukukokerani kumabwalo amilandu?+ 7 Kodi si iwo amene amanyoza+ dzina labwino kwambiri limene mukuimira?+ 8 Tsopano ngati inu mukutsatira lamulo lachifumu+ lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ monga mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu. 9 Koma mukapitiriza kukhala okondera,+ mukuchita tchimo, chifukwa lamulo likukutsutsani+ monga ochimwa.
10 Aliyense wosunga Chilamulo akalakwitsa mbali imodzi, walakwira malamulo onse.+ 11 Pakuti amene anati: “Usachite chigololo,”+ anatinso: “Usaphe munthu.”+ Tsopano ngati iwe sunachite chigololo koma wapha munthu, walakwira chilamulo. 12 Muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la mfulu.+ 13 Pakuti wosachita chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.+ Chifundo n’chopambana kwambiri kuposa chiweruzo.
14 Abale anga, kodi pali phindu lanji ngati wina amati ali ndi chikhulupiriro+ koma sachita ntchito zake?+ Kodi chikhulupiriro chimenecho chingamupulumutse?+ 15 Ngati m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe chakudya chokwanira pa tsikulo,+ 16 koma wina mwa inu n’kunena kuti: “Yendani bwino, mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,” koma osamupatsa zimene thupi lake likusowazo, kodi pali phindu lanji?+ 17 Momwemonso chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake,+ ndi chakufa.
18 Koma wina anganene kuti: “Iweyo uli ndi chikhulupiriro, koma ine ndili ndi ntchito zake. Undionetse chikhulupiriro chako popanda ntchito zake, ndipo ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa mwa ntchito.”+ 19 Umakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi, si choncho?+ Ukuchita bwino. Koma ziwanda nazonso zimakhulupirira ndipo zimanjenjemera.+ 20 Mbuli iwe, kodi sukudziwa kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake n’chopanda pake? 21 Kodi Abulahamu atate wathu+ sanayesedwe wolungama chifukwa cha ntchito zake, atapereka Isaki mwana wake nsembe paguwa?+ 22 Waonatu kuti chikhulupiriro chake chinayendera limodzi ndi ntchito zake, ndipo mwa ntchito zakezo chikhulupiriro chakecho chinakhala changwiro.+ 23 Choncho linakwaniritsidwa lemba limene limati, “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova,* ndipo anaonedwa ngati wolungama,”+ choncho anatchedwa “bwenzi la Yehova.”+
24 Mukuonatu kuti munthu amaonedwa ngati wolungama+ chifukwa cha ntchito zake,+ osati chifukwa cha chikhulupiriro chokha.+ 25 N’chimodzimodzinso ndi Rahabi.+ Kodi Rahabi hule lija, silinaonedwe ngati lolungama chifukwa cha ntchito zake, powalandira bwino azondi aja ndi kuwabweza kwawo powasonyeza njira ina?+ 26 Ndithudi, monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalira lakufa,+ nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.+
3 Abale anga, pasakhale aphunzitsi ambiri pakati panu,+ podziwa kuti tidzalandira chiweruzo chachikulu.+ 2 Paja tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.+ Ngati wina sapunthwa pa mawu,+ ameneyo ndi munthu wangwiro,+ ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse. 3 Tikamangirira zingwe+ pakamwa pa mahatchi* kuti atimvere,+ timatha kulamuliranso matupi awo onse. 4 N’chimodzimodzinso ngalawa. Ngakhale kuti ndi zazikulu kwambiri ndipo zimayenda mokankhidwa ndi mphepo zamphamvu, munthu woziyendetsa amaziwongolera ndi thabwa laling’ono+ kuti zipite kumene iye akufuna.
5 N’chimodzimodzinso lilime. Lilime ndi kachiwalo kakang’ono, koma limadzitama kwambiri.+ Tangoganizani mmene kamoto kakang’onong’ono kamayatsira nkhalango yaikulu. 6 Lilimenso ndi moto.+ Mwa ziwalo zathu zonse, lilime ndilo lili lodzaza ndi zosalungama chifukwa limadetsa thupi lonse.+ Lili ndi moto wa Gehena* ndipo limayatsa moyo wonse wa munthu. 7 Pakuti anthu akhala akuweta mtundu uliwonse wa nyama zakutchire, mbalame, ndi zokwawa ndiponso zamoyo zam’nyanja.+ 8 Koma lilime, palibe munthu ndi mmodzi yemwe angathe kuliweta. Ndilo kanthu kamodzi kosalamulirika ndi kovulaza, kodzaza ndi poizoni wakupha.+ 9 Pakuti lilime timatamanda nalo Yehova,+ amenenso ndi Atate,+ komanso ndi lilime lomwelo timatemberera+ anthu amene analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.”+ 10 Pakamwa pamodzimodzipo pamatuluka mawu otamanda ndi otemberera.
N’kosayenera abale anga kuti zinthu zimenezi zipitirire kuchitika motere.+ 11 Kasupe+ satulutsa madzi abwino ndi owawa padzenje limodzi, amatero ngati? 12 Abale anga, kodi mkuyu ungabale maolivi, kapena mtengo wa mpesa ungabale nkhuyu?+ Ngakhale madzi amchere sangatulutse madzi abwino.
13 Kodi pakati panu pali aliyense wanzeru ndi womvetsa zinthu? Ameneyo ayenera kukhala ndi khalidwe labwino limene limasonyeza kuti amachita chilichonse+ mofatsa ndipo kufatsa kwake kumachokera mu nzeru. 14 Koma ngati m’mitima mwanu muli nsanje yaikulu+ ndi kukonda mikangano,+ musadzitamande+ pakuti kutero n’kunamizira choonadi.+ 15 Imeneyo si nzeru yochokera kumwamba,+ koma ya padziko lapansi,+ yauchinyama ndiponso yauchiwanda.+ 16 Pakuti pamene pali nsanje+ ndi mtima wokonda mikangano, palinso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.+
17 Koma nzeru+ yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera,+ kenako yamtendere,+ yololera,+ yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino,+ yopanda tsankho,+ ndiponso yopanda chinyengo.+ 18 Komanso, chilungamo+ ndicho chipatso+ cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere+ amafesa mu mtendere.+
4 Kodi nkhondo zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Nanga kukangana pakati panu kukuchokera kuti? Kodi sizikuchokera m’zilakolako za thupi lanu+ zimene zikuchita nkhondo m’ziwalo zanu?+ 2 Mumalakalaka, koma simukhala nazo. Mumapha anthu+ ndiponso mumasirira mwansanje,+ koma simupeza kanthu. Mumakangana+ ndiponso mumachita nkhondo. Simukhala ndi kanthu chifukwa simupempha. 3 Mumapempha koma simulandira, chifukwa mukupempha ndi cholinga choipa,+ kuti mukhutiritse zilakolako za matupi anu.+
4 Achigololo+ inu, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu?+ Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi+ la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.+ 5 Kapena mukuyesa kuti lemba limanena pachabe kuti: “Mzimu umene uli mwa ife uli ndi chizolowezi cholakalaka zinthu zosiyanasiyana”?+ 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+
7 Choncho gonjerani+ Mulungu, koma tsutsani Mdyerekezi+ ndipo adzakuthawani.+ 8 Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.+ Yeretsani manja anu ochimwa inu,+ ndipo yeretsani mitima yanu,+ okayikakayika inu.+ 9 Imvani chisoni ndipo lirani.+ Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chisangalalo chanu chisanduke chisoni.+ 10 Dzichepetseni pamaso pa Yehova,+ ndipo iye adzakukwezani.+
11 Abale, muleke kunenerana zoipa.+ Wonenera m’bale wake zoipa kapena woweruza+ m’bale wake, akunenera zoipa lamulo ndi kuweruza lamulo. Choncho ngati ukuweruza lamulo, sukuchita zimene lamulo limanena ayi. Ukukhala woweruza.+ 12 Komatu wopereka lamulo ndi woweruza alipo mmodzi yekha,+ amenenso akhoza kupulumutsa ndi kuwononga.+ Ndiye iwe ndiwe ndani, kuti uziweruza mnzako?+
13 Tamverani tsopano inu amene mumati: “Lero kapena mawa tipita kumzinda wakutiwakuti ndipo tikatha chaka kumeneko. Tikachita malonda kumeneko ndi kupeza phindu.”+ 14 Mumatero chonsecho simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.+ Pakuti ndinu nkhungu yongoonekera kanthawi kenako n’kuzimiririka.+ 15 M’malomwake, muyenera kunena kuti: “Yehova akalola,+ tikhala ndi moyo, ndi kuchita zakutizakuti.”+ 16 Koma tsopano mumakonda kudzitama.+ Kunyada konse koteroko ndi koipa. 17 Chotero, ngati munthu akudziwa kuchita chabwino koma sakuchichita,+ akuchimwa.+
5 Tamverani tsopano inu anthu achuma.+ Lirani, fuulani chifukwa cha masautso amene akubwera kwa inu.+ 2 Chuma chanu chawola, ndipo malaya anu akunja adyedwa ndi njenjete.*+ 3 Golide ndi siliva wanu wadyedwa ndi dzimbiri, ndipo dzimbiri limenelo lidzakhala umboni wokutsutsani. Lidzadya mnofu wa matupi anu. Zimene mwaunjika+ m’masiku otsiriza+ zili ngati moto.+ 4 Tamverani! Malipiro a anthu amene anagwira ntchito+ yokolola m’minda yanu, amene inu simunapereke,+ akufuula ndipo kufuula kwa okololawo kofuna thandizo+ kwafika m’makutu+ a Yehova wa makamu. 5 Mwalidyerera dziko lapansi ndipo mwasangalala.+ Mwanenepetsa mitima yanu pa tsiku lokaphedwa.+ 6 Mwaweruza ndi kupha munthu wolungama. Iye akukutsutsani.+
7 Choncho lezani mtima abale, kufikira kukhalapo*+ kwa Ambuye. Ganizirani mmene amachitira mlimi. Iye amayembekezerabe zipatso zofunika kwambiri zotuluka m’nthaka. Amakhala wodekha mpaka itagwa mvula yoyamba ndi mvula yomaliza.+ 8 Nanunso khalani oleza mtima.+ Limbitsani mitima yanu, chifukwa kukhalapo kwa Ambuye kwayandikira.+
9 Musamang’ung’udzirane abale, kuopera kuti mungaweruzidwe.+ Taonani, Woweruza waima pakhomo.+ 10 Abale, pa nkhani ya kumva zowawa+ ndi kuleza mtima,+ tengerani chitsanzo+ kwa aneneri+ amene analankhula m’dzina la Yehova.+ 11 Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawatcha odala.+ Munamva za kupirira kwa Yobu+ ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa,+ mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.+
12 Koma koposa zonse abale anga, lekani kulumbira, kaya motchula kumwamba kapena dziko lapansi kapena lumbiro lina lililonse.+ Koma tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi, kuti musaweruzidwe.+
13 Kodi pali aliyense mwa inu amene akumva zowawa? Apitirize kupemphera.+ Kodi pali wina amene akukondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.+ 14 Kodi pali wina amene akudwala pakati panu?+ Aitane akulu a mpingo,+ ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta+ m’dzina la Yehova. 15 Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo,+ ndipo Yehova adzamulimbitsa.+ Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.+
16 Choncho muululirane machimo anu poyera+ ndi kupemphererana, kuti muchiritsidwe.+ Pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.+ 17 Eliya anali munthu monga ife tomwe,+ komabe anapemphera kuti mvula isagwe,+ ndipo mvula sinagwe kumeneko kwa zaka zitatu ndi miyezi 6. 18 Anapempheranso, ndipo mvula inagwa kuchokera kumwamba. Nthaka inatulutsa zipatso zake.+
19 Abale anga, ngati wina mwa inu wasocheretsedwa pa choonadi wina n’kumubweza,+ 20 dziwani kuti amene wabweza wochimwa panjira yake yoipa,+ adzapulumutsa moyo wa wochimwayo ku imfa+ ndipo adzakwirira machimo ambiri.+
Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
Onani Zakumapeto 2.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Onani Zakumapeto 6.
Mawu amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
Onani Zakumapeto 8.