2 Mbiri
6 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anati:+ “Yehova anati adzakhala mumdima wandiweyani.+ 2 Koma ine ndakumangirani nyumba yomwe ndi malo anu okhalamo okwezeka,+ malo okhazikika oti mukhalemo mpaka kalekale.”+
3 Kenako mfumu inatembenuka n’kuyang’ana anthuwo. Ndiyeno inayamba kudalitsa+ mpingo wonse wa Isiraeli. Pamenepo n’kuti mpingo wonse wa Isiraeli utaimirira.+ 4 Mfumuyo inapitiriza kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene analankhula ndi pakamwa pake kwa Davide bambo anga,+ ndipo ndi manja ake wakwaniritsa+ zimene ananena, kuti, 5 ‘Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa anthu anga m’dziko la Iguputo, sindinasankhe mzinda m’mafuko onse a Isiraeli woti iwo amangeko nyumba ya dzina langa+ kuti likhale kumeneko, ndipo sindinasankhe munthu woti akhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+ 6 Koma ndidzasankha Yerusalemu+ kuti dzina langa likhale kumeneko, ndiponso ndidzasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’+ 7 Ndipo bambo anga Davide, anafuna mumtima mwawo kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 8 Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Popeza unafuna mumtima mwako kumanga nyumba ya dzina langa, unachita bwino chifukwa unafuna mumtima mwako kuchita zimenezi.+ 9 Koma iweyo sumanga nyumbayi,+ m’malomwake mwana wako wamwamuna wotuluka m’chiuno mwako ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 10 Yehova anakwaniritsa mawu+ amene ananena, kuti ineyo ndilowe m’malo mwa Davide bambo anga+ n’kukhala pampando wachifumu+ wa Isiraeli, monga momwe Yehova ananenera,+ ndiponso kuti ndimange nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 11 Komanso kuti m’nyumbamo ndiikemo Likasa,+ lomwe muli pangano la Yehova limene anapangana ndi ana a Isiraeli.”+
12 Tsopano Solomo anaimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova patsogolo pa mpingo wonse wa Isiraeli.+ Kenako anatambasula manja ake.+ 13 (Pakuti Solomo anapanga nsanja+ yamkuwa n’kuiika pakati pa bwalo lamkati.+ Nsanjayo inali yaikulu mikono isanu m’litali, mikono isanu m’lifupi, ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba inali yaitali mikono itatu. Iye anaimirira pansanjayo.) Atatero anagwada+ patsogolo pa mpingo wonse wa Isiraeli. Kenako anatambasula manja ake n’kuwakweza kumwamba.+ 14 Ndiyeno anayamba kulankhula kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Atumiki anu amene akuyenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse, inu mumawasungira pangano+ ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha.+ 15 Mwakwaniritsa lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga.+ Munalonjeza ndi pakamwa panu ndipo lero mwakwaniritsa ndi dzanja lanu.+ 16 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, sungani lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a m’banja lako sadzasiya kukhala pamaso panga pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Chofunika n’choti ana ako+ asamale mayendedwe awo mwa kuyenda motsatira malamulo anga+ monga momwe iwe wayendera pamaso panga.’+ 17 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ lonjezo lanu+ limene munalonjeza mtumiki wanu Davide likwaniritsidwe.+
18 “Koma kodi Mulungu angakhaledi ndi anthu padziko lapansi?+ Taonani! Kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, simungakwaneko.+ Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?+ 19 Mutembenukire ku pemphero la mtumiki wanu+ ndi pempho lake lopempha chifundo,+ inu Yehova Mulungu wanga. Mverani kulira kwanga kochonderera+ ndi pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu.+ 20 Maso anu akhale akuyang’ana+ nyumba ino usana ndi usiku. Akhale akuyang’ana malo amene munanena kuti mudzaikako dzina lanu,+ mwa kumvetsera pemphero limene mtumiki wanu akupemphera atayang’ana malo ano.+ 21 Mumve mapemphero ochonderera a mtumiki+ wanu ndi a anthu anu Aisiraeli, pamene akupemphera atayang’ana malo ano.+ Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ ndipo mumve n’kukhululuka.+
22 “Munthu akachimwira mnzake+ n’kuchita lumbiro lokhala ndi temberero+ potsimikiza kuti sanachimwe, iye n’kubwera pamaso pa guwa lansembe m’nyumba ino ali pansi pa tembererolo,+ 23 inu mumve muli kumwamba+ ndipo muchitepo kanthu+ mwa kusonyeza amene ali wolakwa pom’bwezera temberero lake,+ ndi kusonyeza amene ali wolungama+ pom’patsa mphoto malinga ndi chilungamo chake.+
24 “Anthu anu Aisiraeli akagonja kwa mdani wawo+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno akabwerera+ kwa inu n’kutamanda dzina lanu+ ndi kupemphera+ ndiponso kupempha kuti muwachitire chifundo pamaso panu m’nyumba ino,+ 25 inuyo mumve muli kumwamba+ ndipo mukhululuke+ tchimo la anthu anu Aisiraeli, ndi kuwabwezeretsa+ kudziko limene munapatsa iwo ndi makolo awo.+
26 “Kumwamba kukatsekeka, mvula n’kumakanika kugwa+ chifukwa choti anali kukuchimwirani,+ ndiyeno iwo n’kupemphera atayang’ana malo ano,+ ndi kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya tchimo lawo chifukwa choti mwakhala mukuwasautsa,+ 27 inuyo mumve muli kumwamba ndipo mukhululuke tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisiraeli, popeza mumawaphunzitsa+ njira yabwino+ yoti ayendemo. Mubweretse mvula+ padziko lanu, limene mwapatsa anthu anu monga cholowa.+
28 “M’dzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu,+ matenda a mbewu a chuku,+ dzombe,+ mphemvu,+ komanso adani+ awo akawaukira m’zipata za mizinda yawo,+ ndiponso kukagwa mliri wamtundu wina uliwonse, nthenda yamtundu wina uliwonse,+ 29 ndiyeno anthuwo akapereka pemphero lililonse,+ pempho lililonse lopempha chifundo+ limene munthu aliyense kapena anthu anu onse Aisiraeli+ angapemphe, chifukwa aliyense wa iwo akudziwa mliri wake+ ndi ululu wake, ndipo aliyense akatambasula manja ake kuwalozetsa kunyumba ino,+ 30 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu. Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inu nokha ndiye mumadziwa bwino mtima wa ana a anthu).+ 31 Muchite zimenezi n’cholinga choti iwo akuopeni,+ mwa kuyenda m’njira zanu masiku onse amene angakhale ndi moyo padziko limene munapatsa makolo athu.+
32 “Komanso mlendo amene sali mmodzi wa anthu anu Aisiraeli,+ amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu,+ ndi dzanja lanu lamphamvu+ ndi mkono wanu wotambasuka,+ ndipo iwo abwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino,+ 33 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani.+ Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu,+ kuti akuopeni+ mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, ndiponso kuti adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.+
34 “Anthu anu akapita ku nkhondo+ kukamenyana ndi adani awo kumene inuyo mwawatumiza,+ ndipo akapemphera+ kwa inu atayang’ana kumzinda umene mwasankha ndi kunyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 35 inuyo mumve muli kumwamba pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo,+ ndipo muwachitire chilungamo.+
36 “Anthu anu akakuchimwirani+ (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu n’kuwakwiyira, n’kuwapereka kwa mdani, adani awowo n’kuwagwira kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ 37 ndiyeno iwo akazindikira kulakwa kwawo m’dziko limene anawatengeralo n’kulapa, ndipo akapempha chifundo kwa inu m’dziko limene akukhalamo monga anthu ogwidwa,+ n’kunena kuti, ‘Tachimwa,+ tachita zolakwa,+ ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 38 n’kubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, m’dziko limene akukhalamo monga anthu ogwidwa,+ m’dziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayang’ana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, kumzinda umene mwasankha+ ndiponso kunyumba ya dzina lanu imene ndamangayi,+ 39 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika.+ Mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo,+ ndipo muwachitire chilungamo.+ Mukhululukire+ anthu anu amene akuchimwirani.
40 “Tsopano Mulungu wanga, chonde, maso anu aone,+ ndipo makutu anu+ akhale tcheru kumvetsera pemphero lokhudza malo ano. 41 Tsopano inu Yehova Mulungu nyamukani+ mulowe mu mpumulo wanu,+ inuyo ndi Likasa limene mumasonyezera mphamvu zanu.+ Ansembe anu, inu Yehova Mulungu, avale chipulumutso ndipo okhulupirika anu asangalale chifukwa cha zabwino.+ 42 Inu Yehova Mulungu, musakane wodzozedwa wanu.+ Musaiwale kukoma mtima kosatha kumene munasonyeza Davide mtumiki wanu.”+