Yesaya
37 Mfumu Hezekiya itangomva zimenezi, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli.+ Kenako inapita m’nyumba ya Yehova.+ 2 Komanso inatuma Eliyakimu+ amene anali woyang’anira banja la mfumu, Sebina mlembi,+ ndi akuluakulu a ansembe,+ onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+ 3 Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa+ ndi lodzudzula, tsiku la mnyozo ndi mwano.+ Tili ngati mkazi amene watsala pang’ono kubereka, koma alibe mphamvu zoti aberekere.+ 4 Mwina Yehova Mulungu amva mawu onse a Rabisake,+ amene mbuye wake mfumu ya Asuri yamutuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira amene alipo.’”+
5 Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.+ 6 Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki+ a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza. 7 Ndiika maganizo+ mwa iye, kuti akamva nkhani inayake,+ abwerere kudziko lake. Ndipo mosalephera, ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga m’dziko lake.”’”+
8 Rabisake+ anali atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi,+ choncho anabwerera kwa mfumuyo n’kukaipeza ikumenyana ndi Libina.+ 9 Tsopano mfumuyo inamva kuti Tirihaka+ mfumu ya Itiyopiya wabwera kudzamenyana nayo. Itangomva zimenezo, nthawi yomweyo inatumizanso amithenga+ kwa Hezekiya n’kuwauza kuti: 10 “Amuna inu mukamuuze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Usalole Mulungu wako amene ukumudalira kuti akunamize,+ ponena kuti: “Yerusalemu saperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11 Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachita kumayiko onse mwa kuwawononga.+ Ndiye kodi iweyo ukuona ngati upulumuka?+ 12 Kodi milungu+ ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawalanditsa?+ Kodi inalanditsa Gozani,+ Harana,+ Rezefi ndi ana a Edeni+ amene anali ku Tela-sara? 13 Ili kuti mfumu ya Hamati,+ mfumu ya Aripadi,+ ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu,+ Hena, ndi Iva?’”+
14 Kenako Hezekiya anatenga kalatayo m’manja mwa amithengawo n’kuiwerenga.+ Pambuyo pake iye anapita nayo kunyumba ya Yehova, n’kuitambasula pamaso pa Yehova.+ 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera kwa Yehova,+ kuti: 16 “Inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+ 17 Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone, ndipo imvani mawu onse a Senakeribu+ amene watumiza kudzatonza nawo Mulungu wamoyo.+ 18 N’zoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko onse, ndi dziko lawo lomwe.+ 19 Atentha milungu yawo pamoto,+ chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga.+ 20 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ tipulumutseni m’manja mwake,+ kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+
21 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti wapemphera kwa ine za Senakeribu mfumu ya Asuri,+ 22 awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:
“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza ndipo wakuseka.+
Kumbuyo kwako, mwana wamkazi wa Yerusalemu wakupukusira mutu.+
23 Kodi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumulankhula monyoza?+
Ndipo ndani amene iwe wam’kwezera mawu,+
Ndi kum’kwezera maso ako m’mwamba?+
Ndi Woyera wa Isiraeli!+
24 Kudzera mwa antchito ako watonza Yehova ndipo wanena kuti,+
Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+
Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+
Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+
Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+
Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+
25 Ndithu ineyo ndidzakumba zitsime ndi kumwa madzi,
Ndidzaumitsa ndi mapazi anga ngalande zonse zamadzi za mtsinje wa Nailo+ wa ku Iguputo.’+
26 Kodi sunamve?+ Kuyambira nthawi zakale izi n’zimene ndidzachite.+
Ndinakonza zimenezi kuyambira masiku amakedzana.+ Tsopano ndizichita.+
Iweyo udzagwira ntchito yosandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, kukhala yopanda anthu ngati milu ya mabwinja.+
Adzakhala ngati zomera zakutchire, ndi udzu wanthete wobiriwira,+
Ngati udzu womera padenga+ ndiponso wa m’mizere ya m’munda, ukawauka ndi mphepo yotentha yakum’mawa.+
28 Ukakhala phee, ukamatuluka,+ ndiponso ukamalowa, ine ndimadziwa bwino,+
Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+
29 Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga.+
Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+
Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+
30 “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu: Chaka chino mudya mbewu zomera zokha zimene zinagwera pansi.+ Chaka chamawa mudzadya mbewu zongomera zokha, koma chaka chamkuja, anthu inu mudzabzale mbewu n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+ 31 Anthu a m’nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ 32 Chifukwa anthu otsala adzachoka ku Yerusalemu,+ ndipo opulumuka adzachoka kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
33 “‘Chotero Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+ “Sadzalowa mumzinda uno,+ kapena kuponyamo muvi, kapena kufikamo ndi chishango, kapenanso kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo pafupi ndi mpanda wa mzindawu atauzungulira.”’+
34 “‘Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera, ndipo sadzalowa mumzinda uno,’ ndiwo mawu a Yehova.+ 35 ‘Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’”+
36 Ndiyeno mngelo+ wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.+ Anthu podzuka m’mawa, anangoona kuti onse aja ndi mitembo yokhayokha.+ 37 Choncho Senakeribu+ mfumu ya Asuri anachokako n’kubwerera+ kukakhala ku Nineve.+ 38 Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.