Yobu
36 Elihu anapitiriza kunena kuti:
2 “Ndilezereni mtima kwa kanthawi kochepa ndipo ndikuuzani
Kuti mawu alipobe oti ndinene m’malo mwa Mulungu.
3 Zimene ndinene ndizitenga kutali,
Ndipo ndilengeza kuti amene anandipanga, ndiye mwiniwake wa chilungamo.+
5 Mulungutu ndi wamphamvu+ ndipo sadzakana munthu.
Iye ali ndi mphamvu zazikulu zomvetsa zinthu.
6 Iye sadzasiya woipa aliyense ali wamoyo,+
Koma adzapereka chiweruzo cholungama kwa osautsika.+
7 Sadzachotsa maso ake pa aliyense wolungama.+
Adzaika mafumu pamipando yachifumu,+
Adzawachititsa kuti alamulire kwamuyaya, ndipo iwo adzakhala ndi mphamvu zambiri.
9 Ndiyeno iye adzawauza za momwe iwo amachitira zinthu
Ndiponso zolakwa zawo, chifukwa iwo amadzikuza.
10 Iye adzatsegula makutu awo kuti iwo amve pamene iye akuwalimbikitsa,+
Ndipo adzawauza kuti asiye kuchita zopweteka ena.+
15 Iye adzapulumutsa wozunzika m’masautso ake,
Ndipo adzatsegula makutu awo pamene akuponderezedwa.
16 Ndithu iye adzakukopani n’kukuchotsani pakamwa pa zowawa.+
M’malomwake padzakhala malo otakasuka,+ osati opanikiza,
Ndipo chitonthozo cha patebulo panu chidzakhala chodzaza ndi mafuta.+
18 Samalani kuti mkwiyo+ usakuchititseni kuwomba m’manja chifukwa cha njiru,
Ndipo dipo lalikulu+ lisakusocheretseni.
19 Kodi kulira kwanu kopempha thandizo kudzakupindulirani?+ Ayi, sikudzakupindulirani ngakhalenso pa mavuto,
Ngakhale muyesetse mwamphamvu bwanji.+
20 Musapumire m’mwamba polakalaka usiku,
Pamene anthu amabwera kuchokera kumene anali.
21 Samalani kuti musabwerere ku zinthu zopweteka ena,+
Chifukwa mwasankha zimenezi m’malo mwa masautso.+
22 Mulungutu amachita zinthu zapamwamba ndi mphamvu zake.
Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye?