Nehemiya
13 Pa tsiku limenelo buku+ la Mose linawerengedwa+ pamaso pa anthuwo. Iwo anapeza kuti m’bukumo analembamo kuti Muamoni+ ndi Mmowabu+ aliyense sayenera kubwera mumpingo wa Mulungu woona mpaka kalekale,+ 2 chifukwa iwowa sanachingamire ana a Isiraeli kuti awapatse chakudya+ ndi madzi.+ M’malomwake, analemba ganyu Balamu+ kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+ 3 Choncho atangomva chilamulocho,+ anayamba kupatula+ khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana kuwachotsa pakati pa Isiraeli.
4 Zimenezi zisanachitike, panali Eliyasibu+ wansembe amene anali kuyang’anira zipinda zodyeramo+ m’nyumba ya Mulungu wathu, ndipo anali wachibale wa Tobia.+ 5 Eliyasibu anakonzera Tobia chipinda chachikulu chodyeramo+ m’chipinda chimene nthawi zonse anali kuikamo nsembe yambewu,+ lubani,* ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda a pazipata anayenera kulandira, komanso zimene anali kupereka kwa ansembe.
6 Nthawi yonseyi ine sindinali mu Yerusalemu, pakuti m’chaka cha 32+ cha ulamuliro wa Aritasasita+ mfumu ya Babulo, ndinabwerera kwa mfumu. Patapita nthawi, ndinapempha mfumuyo kuti ndichoke.+ 7 Ndiyeno ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinaona zoipa zimene Eliyasibu+ anachita mwa kukonzera Tobia+ chipinda m’bwalo la nyumba+ ya Mulungu woona. 8 Zimenezi zinandiipira kwambiri.+ Choncho, katundu yense wa m’nyumba ya Tobia ndinam’ponyera kunja+ kwa chipinda chodyeramo. 9 Zitatero ndinalamula kuti ayeretse+ zipinda zodyeramo+ ndipo anachitadi zomwezo. Kenako ndinabwezera pamalo pake ziwiya+ za nyumba ya Mulungu woona pamodzi ndi zopereka zambewu ndi lubani.+
10 Ndiyeno ndinazindikira kuti magawo+ a Alevi sanali kuperekedwa kwa iwo, moti aliyense wa Aleviwo ndi oimba amene anali kutumikira anathawa ndipo anapita kumunda wake.+ 11 Zitatero ndinayamba kuimba mlandu+ atsogoleriwo+ ndi kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani nyumba ya Mulungu woona yasiyidwa chonchi?”+ Pamenepo ndinawasonkhanitsa pamodzi ndipo ndinawaika pamalo awo ogwirira ntchito. 12 Anthu onse a mu Yuda anabweretsa kumalo osungira zinthu+ chakhumi+ cha mbewu,+ cha vinyo watsopano+ ndiponso cha mafuta.+ 13 Ndiyeno ndinaika Selemiya wansembe, Zadoki wokopera Malemba ndi Pedaya mmodzi mwa Alevi, kuti akhale oyang’anira malo osungira zinthu. Amenewa anali kuyang’anira Hanani mwana wa Zakuri amene anali mwana wa Mataniya,+ pakuti anthu anali kuwaona kuti ndi okhulupirika.+ Iwowa anapatsidwa udindo wogawa+ zinthu kwa abale awo.
14 Mundikumbukire,+ inu Mulungu wanga, chifukwa cha zinthu zimenezi ndipo musaiwale+ ntchito za kukoma mtima kosatha zimene ndachitira nyumba+ ya Mulungu wanga ndi onse otumikira kumeneko.
15 Masiku amenewo ku Yuda ndinaona anthu akuponda moponderamo mphesa tsiku la sabata.+ Anali kubweretsa mbewu ndi kuzikweza+ pa abulu.+ Analinso kukweza pa abuluwo vinyo, mphesa, nkhuyu+ ndi katundu wosiyanasiyana ndipo anali kubwera nazo ku Yerusalemu tsiku la sabata.+ Ine ndinawadzudzula pa tsiku limene anali kugulitsa zinthu zimenezi. 16 Anthu a ku Turo+ anali kukhala mumzindawo ndipo anali kubweretsa nsomba ndi malonda osiyanasiyana.+ Iwo anali kugulitsa zinthu zimenezi pa tsiku la sabata kwa ana a Yuda mu Yerusalemu. 17 Choncho ndinayamba kuimba mlandu anthu olemekezeka+ a ku Yuda kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita zinthu zoipa, mpaka kuipitsa tsiku la sabata? 18 Kodi izi si zimene makolo anu anachita,+ mwakuti Mulungu wathu anadzetsa tsoka lonseli+ pa ife komanso pamzinda uwu? Koma inu mukuwonjezera kuyaka kwa mkwiyo wake pa Isiraeli mwa kuipitsa sabata.”+
19 Ndiyeno mdima utafika pazipata za Yerusalemu, sabata lisanayambe, ndinapereka lamulo ndipo zitseko zinayamba kutsekedwa.+ Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo kufikira sabata litatha. Ndipo ndinaika ena mwa atumiki anga m’zipata kuti munthu asalowe ndi katundu tsiku la sabata.+ 20 Choncho ochita malonda ndi ogulitsa zinthu zosiyanasiyana anagona panja pa Yerusalemu kawiri. 21 Pamenepo ndinawachenjeza+ kuti: “N’chifukwa chiyani mukugona kunja kwa mpanda? Mukachitanso zimenezi ndikukhaulitsani.”+ Kuyambira nthawi imeneyo sanabwerenso pa tsiku la sabata.
22 Ndiyeno ndinauza Alevi+ kuti pobwera azidziyeretsa nthawi zonse+ komanso azilondera zipata za mzinda+ kuti tsiku la sabata likhale loyera.+ Inu Mulungu wanga, mundikumbukirenso+ pa zimenezi ndipo mundimvere chifundo malinga ndi kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.+
23 Komanso ndinaona kuti Ayuda ena anali atakwatira+ akazi achiasidodi,+ achiamoni ndi achimowabu.+ 24 Hafu ya ana awo aamuna anali kulankhula Chiasidodi ndipo palibe amene ankatha kulankhula Chiyuda,+ koma anali kulankhula chinenero cha anthu ena. 25 Ndiyeno ndinayamba kuwaimba mlandu ndi kuwatemberera.+ Ena mwa amuna amenewo ndinawamenya,+ kuwazula tsitsi ndi kuwalumbiritsa pamaso pa Mulungu kuti:+ “Musapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, ndipo musalole kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna kapenanso inuyo.+ 26 Kodi si akazi amenewa amene anachimwitsa Solomo mfumu ya Isiraeli?+ Mwa mitundu yonse panalibe mfumu yofanana naye.+ Iye anakondedwa ndi Mulungu wake,+ mwakuti Mulungu anamuika kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Koma akazi achilendo anamuchimwitsa.+ 27 Kodi si zodabwitsa kuti inunso mukuchita choipa chachikulu chimenechi, mwa kukwatira akazi achilendo, kumene ndi kuchita mosakhulupirika kwa Mulungu wanu?”+
28 Ndiyeno mmodzi mwa ana aamuna a Yoyada,+ mwana wa Eliyasibu,+ mkulu wa ansembe anali mkamwini wa Sanibalati+ wa ku Beti-horoni.+ Choncho ndinamuthamangitsa, kum’chotsa pamaso panga.+
29 Inu Mulungu wanga, akumbukireni amenewa chifukwa anaipitsa+ unsembe ndiponso pangano+ limene munachita ndi ansembe ndi Alevi.+
30 Ndiyeno ndinawayeretsa+ mwa kuchotsa chilichonse chachilendo. Ndinapereka ntchito kwa ansembe ndi Alevi, aliyense ndinam’patsa ntchito yake,+ 31 ngakhale ntchito yobweretsa nkhuni+ pa nthawi zoikidwiratu ndi mbewu zoyamba kucha.
Inu Mulungu wanga, mundikumbukire+ pa zabwino zimene ndinachita.+