2 Mafumu
19 Mfumu Hezekiya+ itangomva zimenezi, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake+ n’kuvala chiguduli.+ Kenako inapita m’nyumba ya Yehova.+ 2 Komanso, inatuma Eliyakimu+ amene anali woyang’anira banja la mfumu, Sebina+ mlembi, ndi akuluakulu a ansembe, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+ 3 Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa+ ndi lodzudzula,+ tsiku la mnyozo ndi mwano.+ Tili ngati mkazi amene watsala pang’ono kubereka,+ koma alibe mphamvu zoti aberekere.+ 4 Mwina Yehova Mulungu amva+ mawu onse a Rabisake, amene mbuye wake mfumu ya Asuri yam’tuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira+ amene alipo.’”
5 Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.+ 6 Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza.+ 7 Ndiika maganizo mwa iye,+ kuti akamva nkhani inayake,+ abwerere kudziko lake. Ndipo mosalephera ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga m’dziko lake.”’”+
8 Koma Rabisake+ anali atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi,+ choncho anabwerera kwa mfumuyo n’kukaipeza ikumenyana ndi Libina.+ 9 Mfumuyo inamva kuti Tirihaka mfumu ya Itiyopiya wabwera kudzamenyana nayo. Choncho inatumizanso amithenga+ kwa Hezekiya n’kuwauza kuti: 10 “Amuna inu mukamuuze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Usalole Mulungu wako amene ukum’dalira kuti akunamize,+ ponena kuti: “Yerusalemu+ saperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11 Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachita kumayiko onse amene anawawononga.+ Ndiye kodi iweyo ukuona ngati upulumuka?+ 12 Kodi milungu+ ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawalanditsa? Kodi inalanditsa Gozani,+ Harana,+ Rezefi ndi ana a Edeni+ amene anali ku Tela-sara?+ 13 Ili kuti mfumu ya Hamati,+ mfumu ya Aripadi,+ ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena, ndi Iva?’”+
14 Kenako Hezekiya anatenga kalatayo m’manja mwa amithengawo n’kuiwerenga.+ Pambuyo pake iye anapita nayo kunyumba ya Yehova n’kukaitambasula pamaso pa Yehova.+ 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera+ pamaso pa Yehova, kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi,+ inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse+ a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba+ ndi dziko lapansi.+ 16 Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone, ndipo imvani mawu a Senakeribu amene watumiza kudzatonza nawo+ Mulungu wamoyo. 17 N’zoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mitundu ndi mayiko awo.+ 18 Atentha milungu yawo pamoto, chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga. 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ chonde tipulumutseni+ m’manja mwake, kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+
20 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya, wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti,+ ‘Ndamva pemphero+ limene wapemphera kwa ine lokhudza Senakeribu mfumu ya Asuri.+ 21 Awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:
“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza+ ndipo wakuseka.+
Kumbuyo kwako, mwana wamkazi wa Yerusalemu+ wakupukusira mutu.+
22 Kodi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumulankhula monyoza?+
Ndipo ndani amene iwe wam’kwezera mawu,+
Ndi kum’kwezera maso ako m’mwamba?+
Ndi Woyera wa Isiraeli!+
23 Kudzera mwa amithenga ako+ watonza Yehova ndipo wanena kuti,+
‘Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+
Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+
Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+
Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza+ italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+
Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+
24 Ndithu ineyo ndidzakumba zitsime ndi kumwa madzi achilendo,
Ndidzaumitsa ndi mapazi anga ngalande zonse zamadzi za mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.’+
25 Kodi sunamve?+ Kuyambira nthawi zakale, izi n’zimene ndidzachite.+
Ndinakonza zimenezi kuyambira masiku amakedzana.+
Tsopano ndizichita.+
Iweyo udzagwira ntchito yosandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, kukhala yopanda anthu ngati milu ya mabwinja.+
26 Anthu okhala m’mizindayo adzafooka manja.+
Adzachita mantha kwambiri ndiponso adzachita manyazi.+
Adzakhala ngati zomera zakutchire, ndi udzu wanthete wobiriwira,+
Ngati udzu womera padenga+ ukawauka ndi mphepo yotentha yakum’mawa.+
27 Ukakhala phee, ukamatuluka,+ ndiponso ukamalowa, ine ndimadziwa bwino,+
Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+
28 Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga,+
Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+
Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+
29 “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu:+ Chaka chino mudya mmera wa mbewu zimene zinagwera pansi.+ M’chaka chachiwiri mudzadya mbewu zongomera zokha, koma m’chaka chachitatu, anthu inu mudzabzale mbewu+ n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa ndi kudya zipatso zake.+ 30 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ 31 Chifukwa anthu otsala adzachokera ku Yerusalemu,+ ndipo opulumuka adzachokera kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
32 “‘N’chifukwa chake Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+ “Sadzalowa mumzinda uno,+ kapena kuponyamo muvi,+ kapena kufikamo ndi chishango, kapenanso kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo* pafupi ndi mpanda wa mzindawu atauzungulira.+ 33 Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera, ndipo sadzalowa mumzinda uno, ndiwo mawu a Yehova.+ 34 Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+
35 Ndiyeno usiku umenewo, mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri+ n’kukapha asilikali 185,000.+ Anthu podzuka m’mawa, anangoona kuti onse aja ndi mitembo yokhayokha.+ 36 Choncho Senakeribu+ mfumu ya Asuri inachokako n’kubwerera+ kukakhala ku Ninive.+ 37 Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.