Kalata Yoyamba kwa Akorinto
1 Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi+ wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu,+ pamodzi ndi Sositene+ m’bale wathu, 2 ndikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto,+ kwa inu amene mwayeretsedwa+ mwa Khristu Yesu, amene mwaitanidwa kuti mukhale oyera,+ pamodzi ndi onse amene kulikonse akuitana pa dzina+ la Ambuye wathu, Yesu Khristu, Ambuye wawo ndiponso wathu.+
3 Kukoma mtima kwakukulu+ ndi mtendere+ zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu+ zikhale ndi inu.
4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu, poona kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu kumene anakusonyezani kudzera mwa Khristu Yesu,+ 5 kuti mwa iye mwakhala olemera+ m’zinthu zonse, pokhala ndi mphamvu zonse za kulankhula ndi kudziwa zinthu zonse,+ 6 popeza kuti umboni wonena za Khristu+ wakhazikika pakati pa inu, 7 moti palibe mphatso+ imene ikuperewera mwa inu, pamene mukudikira mwachidwi kuululidwa+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 8 Mulungu adzakulimbitsani+ mpaka pa mapeto, kuti musakhale ndi chifukwa chokunenezerani+ m’tsiku+ la Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 9 Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale oyanjana+ ndi Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu, ndi wokhulupirika.+
10 Tsopano ndikukudandaulirani+ abale, m’dzina+ la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndi kuti pasakhale magawano+ pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana+ pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ 11 Pakuti a m’banja la Kuloe andiuza+ za inu, abale anga, kuti pali magawano pakati panu. 12 Ndikutanthauza kuti, ena mwa inu amanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena amati, “Ine ndine wa Apolo,”+ enanso amati “Ine ndine wa Kefa,” pamene ena amati, “Ine ndine wa Khristu.” 13 Choncho Khristu wakhala wogawanika.+ Paulo sanapachikidwe chifukwa cha inu, anatero kodi? Kapena kodi munabatizidwa+ m’dzina la Paulo? 14 Ndikusangalala kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo+ ndi Gayo,+ 15 moti wina sanganene kuti munabatizidwa m’dzina langa. 16 Inde, ndinabatizanso banja la Sitefana.+ Koma za enawo, sindikudziwa ngati ndinabatizapo aliyense. 17 Pakuti Khristu sananditume+ kukabatiza anthu, koma kukalengeza uthenga wabwino, osati mwa nzeru za kulankhula,+ kuti mtengo wozunzikirapo* wa Khristu ungakhale wopanda pake.
18 Nkhani yokhudza mtengo wozunzikirapowo ndi chinthu chopusa+ kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,+ koma kwa ife amene tikupulumutsidwa+ ndi mphamvu ya Mulungu.+ 19 Pakuti Malemba amati: “Ndidzathetsa nzeru zonse za anthu anzeru,+ ndipo ndidzakankhira pambali+ kuchenjera kwa anthu ophunzira.”+ 20 Kodi wanzeru ali kuti? Mlembi ali kuti?+ Katswiri wa mtsutso+ wa nthawi* ino ali kuti?+ Kodi Mulungu sanapange nzeru za dzikoli kukhala zopusa?+ 21 Pakuti ngakhale kuti dziko mwa nzeru zake+ silinathe kumudziwa Mulungu,+ kunamukomera Mulungu mwa nzeru zake kupulumutsa okhulupirira kudzera mu nkhani yopusayo,+ imene ikulalikidwa.
22 Pakuti Ayuda amafuna kuona zizindikiro+ ndipo Agiriki amafunafuna nzeru,+ 23 koma ife timalalikira za Khristu amene anapachikidwa.+ Kwa Ayuda, chimenechi ndi chinthu chokhumudwitsa+ ndipo kwa mitundu ina ndi kupusa.+ 24 Ngakhale zili choncho, kwa amene anaitanidwa, Ayuda ndiponso Agiriki, Khristu ndiye mphamvu+ ya Mulungu ndi nzeru+ za Mulungu. 25 Pakuti chinthu chopusa cha Mulungu ndi chanzeru kuposa anthu, ndipo chinthu chofooka cha Mulungu n’champhamvu kuposa anthu.+
26 Mukuona mmene anakuitanirani, abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa,+ si ambiri amphamvu+ amene anaitanidwa, si ambiri a m’mabanja achifumu. 27 Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko+ kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi+ zinthu zamphamvu. 28 Mulungu anasankha zinthu zonyozeka za dziko ndi zinthu zimene anthu amaziona ngati zachabechabe, zinthu zimene palibe,+ kuti athetse+ mphamvu zinthu zimene zilipo, 29 kuti pasapezeke munthu wodzitama+ pamaso pa Mulungu. 30 Koma inu muli ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru+ za Mulungu ndiponso chilungamo+ cha Mulungu. Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+ 31 kuti zikhale monga Malemba amanenera kuti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”+
2 Chotero abale, pamene ndinafika kwa inu kudzalengeza za chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu, sindinafike ndi malankhulidwe+ adzaoneni kapena ndi nzeru zodabwitsa. 2 Pakuti ndinasankha kuti pamene ndili pakati panu ndisadziwe china chilichonse kupatulapo Yesu Khristu,+ amene anapachikidwa. 3 Choncho ndinafika kwa inu ndili wofooka, ndipo ndinali kunjenjemera+ ndi mantha. 4 Polankhula ndi polalikira, mawu anga sanali okopa, oonetsa nzeru, koma oonetsa mzimu ndi mphamvu,+ 5 kuti chikhulupiriro chanu chisazikike pa nzeru za anthu,+ koma pa mphamvu ya Mulungu.+
6 Tsopano tikulankhula za nzeru kwa anthu okhwima mwauzimu,+ koma osati nzeru+ ya nthawi ino kapena ya olamulira a nthawi* ino+ amene adzawonongedwa.+ 7 Koma tikulankhula za nzeru ya Mulungu imene inaonekera m’chinsinsi chopatulika,+ nzeru yobisika. Mulungu anakonzeratu zochita zimenezi kusanakhale nthawi* zosiyanasiyana,+ kuti tikhale ndi ulemerero. 8 Palibe wolamulira+ ndi mmodzi yemwe wa nthawi* ino amene anadziwa+ nzeru imeneyi, chifukwa ngati anali kuidziwa sakanapachika+ Ambuye waulemereroyo. 9 Koma monga mmene Malemba amanenera: “Palibe munthu amene anaonapo kapena kumvapo kapenanso kuganizapo zimene Mulungu wakonzera omukonda.”+ 10 Pakuti mwa mzimu+ wake, Mulungu anaululira+ ifeyo zinthu zimenezi, chifukwa mzimu+ umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama+ za Mulungu.
11 Kodi ndi munthu uti amene angadziwe za munthu kupatulapo mzimu+ umene uli mwa munthuyo? Momwemonso, palibe amene akudziwa zinthu za Mulungu, kupatulapo mzimu+ wa Mulungu. 12 Tsopano sitinalandire mzimu+ wa dziko, koma mzimu+ wochokera kwa Mulungu, kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima.+ 13 Timalankhulanso zinthu zimenezi, osati ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu,+ koma ndi mawu amene mzimu+ watiphunzitsa, pamene tikuphatikiza zochitika zauzimu ndi mawu auzimu.+
14 Koma munthu wokonda zinthu za m’dziko* salandira zinthu za mzimu wa Mulungu, chifukwa amaziona ngati zopusa ndipo sangathe kuzidziwa,+ chifukwa zimafuna kuzifufuza mwauzimu. 15 Komano munthu wauzimu+ amafufuza zinthu zonse, koma iye safufuzidwa+ ndi munthu aliyense. 16 Pakuti “ndani akudziwa maganizo a Yehova+ kuti amulangize?”+ Koma ifeyo tili ndi maganizo+ a Khristu.
3 Chotero abale, sindinathe kulankhula nanu monga anthu auzimu,+ koma monga anthu oganiza ngati anthu a m’dzikoli,* monga tiana+ mwa Khristu. 2 Ndinakupatsani mkaka, osati chakudya chotafuna,+ chifukwa munali musanalimbe mokwanira. Komatu ngakhale tsopano simunalimbebe mokwanira,+ 3 chifukwa mukadali anthu oganiza ngati anthu a m’dzikoli.*+ Kodi ngati mukuchitirana nsanje ndi kukangana nokhanokha,+ sindiye kuti ndinu akuthupi ndipo mukuyenda monga anthu?+ 4 Ngati wina akunena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ndipo wina akunenanso kuti: “Ine ndine wa Apolo,”+ kodi sindiye kuti mukungofanana ndi anthu onse basi?
5 Kodi Apolo ndani?+ Inde, Paulo ndani? Iwo angokhala atumiki+ amene anakuthandizani kukhala okhulupirira, malinga ndi ntchito imene Ambuye anagawira aliyense wa iwo. 6 Ineyo ndinabzala,+ Apolo anathirira,+ koma Mulungu ndiye anakulitsa.+ 7 Chotero wobzala+ kapena wothirira sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.+ 8 Choncho wobzala ndi wothirira ali amodzi,+ koma aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake.+ 9 Pakuti ndife antchito anzake a Mulungu.+ Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa,+ nyumba ya Mulungu.+
10 Malinga ndi kukoma mtima kwakukulu+ kumene Mulungu anandisonyeza, ndinayala maziko+ monga woyang’anira wanzeru wa ntchito zomangamanga, koma amene akumanga pamaziko amenewo ndi munthu wina. Aliyense asamale mmene akumangirapo.+ 11 Pakuti palibe munthu wina amene angayale maziko ena+ alionse kupatulapo amene anayalidwawo, omwe ndi Yesu Khristu.+ 12 Tsopano ngati munthu akumanga pamazikowo ndi golide, siliva, miyala yamtengo wapatali, mitengo, udzu ndi ziputu, 13 ntchito ya wina aliyense idzaonekera. Pakuti tsikulo lidzasonyeza ntchitoyo poyera, chifukwa moto ndiwo udzaonetsa zimenezo poyera,+ ndipo motowo udzaonetsa kuti ntchito ya munthu aliyense ndi yotani. 14 Ngati ntchito imene munthu wamanga pamazikowo idzakhalapobe,+ iye adzalandira mphoto.+ 15 Ngati ntchito ya munthu idzatenthedwa ndi moto, ndiye kuti zake zatayika, koma iyeyo adzapulumuka.+ Koma ngakhale adzatero, adzakhala ngati wapulumuka pamoto.+
16 Kodi inu simukudziwa kuti ndinu kachisi wa Mulungu,+ ndi kuti mzimu wa Mulungu ukukhala mwa inu?+ 17 Ngati munthu aliyense wawononga kachisi wa Mulungu, Mulungu adzawononganso munthu ameneyo,+ pakuti kachisi wa Mulungu ndi woyera,+ ndipo kachisiyo+ ndinuyo.+
18 Munthu asamadzinyenge yekha: Ngati aliyense wa inu akudziyesa wanzeru+ mu nthawi* ino, akhale wopusa kuti akhale wanzeru.+ 19 Pakuti kwa Mulungu nzeru za m’dzikoli n’zopusa,+ chifukwa Malemba amati: “Iye amakola anzeru m’kuchenjera kwawo.”+ 20 Ndiponso: “Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu anzeru ndi opanda pake.”+ 21 Chotero pasakhale munthu wodzitama chifukwa cha anthu, popeza zinthu zonse ndi zanu,+ 22 kaya Paulo, Apolo,+ Kefa, dziko, moyo, imfa, zinthu zimene zilipo tsopano kapena zimene zidzakhalapo,+ zonse ndi zanu. 23 Inuyo ndinu ake a Khristu,+ ndipo Khristu ndi wa Mulungu.+
4 Chotero anthu azitha kuona kuti ndife atumiki+ a Khristu ndi oyang’anira+ zinsinsi zopatulika+ za Mulungu. 2 Komanso pamenepa, chofunika kwa woyang’anira+ ndicho kukhala wokhulupirika.+ 3 Tsopano zonena kuti ndiweruzidwe ndi inu kapena ndi bwalo lina lililonse la anthu+ si nkhani kwa ine. Ngakhale ine ndemwe sindidziweruza ndekha. 4 Pakuti sindikudziwa+ kanthu kalikonse konditsutsa mumtima mwanga. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti basi ndine wolungama, koma Yehova ndiye amandifufuza.+ 5 Chotero musaweruze+ kalikonse nthawi isanakwane, mpaka Ambuye adzafike.+ Akadzafika adzaunika zinsinsi za mu mdima+ ndi kuonetsa poyera+ zolingalira za m’mitima, ndipo aliyense adzatamandidwa yekha ndi Mulungu.+
6 Tsopano abale, zinthu zimenezi ndazinena monga zochitika kwa ine mwini ndi Apolo+ kuti inuyo mupindule, kuti muphunzire kwa ife lamulo ili lakuti: “Musapitirire zinthu zolembedwa,”+ kuti aliyense wa inu asadzitukumule+ pokonda munthu wina n’kudana ndi wina.+ 7 Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana+ ndi ena ndani? Inde, uli ndi chiyani chimene sunachite kulandira?+ Ndiye ngati unachita kulandira zinthu zimenezo,+ n’chifukwa chiyani ukudzitama+ ngati kuti sunachite kulandira?
8 Kodi anthu inu mwakhuta kale eti? Mwalemera kale, si choncho?+ Kodi mwayamba kale kulamulira monga mafumu+ popanda ife? Ndikanakondadi mukanayamba kulamulira monga mafumu, kuti ifenso tilamulire limodzi nanu monga mafumu.+ 9 Pakuti ndikuona ngati Mulungu waika atumwife kukhala ngati omalizira pachionetsero+ monga anthu okaphedwa,+ chifukwa takhala ngati choonetsedwa m’bwalo la masewera+ kudziko, kwa angelo,+ ndi kwa anthu.+ 10 Takhala opusa+ chifukwa cha Khristu, koma inu mwakhala ochenjera+ mwa Khristu. Ife ndife ofooka,+ inu ndinu amphamvu.+ Inu muli ndi mbiri yabwino,+ koma ifeyo tikunyozedwa.+ 11 Mpaka pano tikadali anjala+ ndi aludzu+ ndi ausiwa.+ Tikuzunzidwabe,+ tikusowabe pokhala,+ 12 ndipo tikugwirabe ntchito yolimba+ ndi manja athu.+ Pamene akutinenera zachipongwe, timadalitsa.+ Pozunzidwa, timapirira.+ 13 Ponyozedwa, timayankha mofatsa.+ Mpaka tsopano, takhala ngati zinyalala za dziko, nyansi za zinthu zonse.+
14 Sikuti ndikulemba zinthu zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni monga ana anga okondedwa.+ 15 Pakuti ngakhale mutakhala ndi aphunzitsi+ 10,000 mwa Khristu, ndithudi mulibe abambo ambiri,+ pakuti mwa Khristu Yesu ndakhala bambo anu kudzera mwa uthenga wabwino.+ 16 Chotero ndikukuchondererani, tsanzirani ineyo.+ 17 Ndiye chifukwa chake ndikukutumizirani Timoteyo,+ popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika+ mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu,+ monga mmenenso ineyo ndikuphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse.
18 Ena amadzitukumula+ ngati kuti sindidzabwera n’komwe kwanuko. 19 Koma ndifika kwanuko posachedwapa, Yehova akalola,+ ndipo sindidzafuna kumva mawu a odzitukumulawo, koma ndidzafuna ndione mphamvu yawo. 20 Pakuti ufumu wa Mulungu sunagone m’mawu, koma mu mphamvu.+ 21 Kodi mukufuna chiyani? Mukufuna ndibwere kwa inu ndi chikwapu,+ kapena ndi chikondi ndi mzimu wofatsa?+
5 Mbiri yamvekatu kuti pakuchitika dama*+ pakati panu, ndipo dama lake ndi loti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.+ 2 Kodi mukudzitukumula,+ m’malo mwa kumva chisoni,+ kuti munthu amene anachita zimenezi achotsedwe pakati panu?+ 3 Ineyo pandekha, ngakhale kuti mwa thupi sindili kumeneko koma mu mzimu ndili komweko, ndamuweruza kale+ ndithu munthu amene wachita zimenezi, ngati kuti ndinali nanu kumeneko. 4 Ndaweruza kuti m’dzina la Ambuye wathu Yesu, mukakumana pamodzi, komanso ndi mzimu wanga ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,+ 5 mupereke munthu ameneyu kwa Satana+ kuti thupilo liwonongedwe, n’cholinga choti mzimuwo+ upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye.+
6 Chimene mukudzitamira+ si chabwino ayi. Kodi simukudziwa kuti chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa+ mtanda wonse?+ 7 Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano,+ popeza ndinu opanda chofufumitsa. Pakuti Khristu+ waperekedwa+ monga nsembe yathu ya pasika.+ 8 Chotero tiyeni tichite chikondwererochi,+ osati ndi chofufumitsa chakale,+ kapena chofufumitsa+ choimira zoipa ndi uchimo,+ koma ndi mikate yopanda chofufumitsa yoimira kuona mtima ndi choonadi.+
9 M’kalata yanga ndinakulemberani kuti muleke kuyanjana ndi anthu adama. 10 Sindikutanthauza kuti muzipeweratu adama+ a m’dzikoli,+ kapena aumbombo ndi olanda, kapena opembedza mafano ayi. Kuti muchite zimenezo, ndiye mungafunikire kutuluka m’dzikomo.+ 11 Koma tsopano ndikukulemberani kuti muleke kuyanjana+ ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo,+ kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa,+ kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi. 12 Nanga kuweruza anthu amene ali kunja*+ ndi ntchito yanga ngati? Kodi inu si paja mumaweruza amene ali mkati,+ 13 ndipo Mulungu amaweruza amene ali kunja?+ “M’chotseni pakati panu munthu woipayo.”+
6 Kodi wina wa inu akakhala ndi mlandu+ ndi mnzake, amalimba mtima bwanji kupita kukhoti kwa anthu osalungama,+ osati kwa oyerawo?+ 2 Kapena simukudziwa kuti oyerawo adzaweruza+ dziko?+ Ndipo ngati mudzaweruza dziko, kodi simungathe kuzenga milandu yaing’ono kwambiri+ ngati imeneyo? 3 Kodi simukudziwa kuti tidzaweruza angelo?+ Ndiye tingalephere bwanji kuweruza nkhani za m’moyo uno? 4 Chotero, ngati muli ndi nkhani zofuna kuweruza+ m’moyo uno, kodi anthu amene mpingo suwayesa kanthu ndiwo mukuwaika kukhala oweruza?+ 5 Ndikulankhula choncho kuti ndikuchititseni manyazi.+ Kodi zoona palibe wanzeru ndi mmodzi yemwe+ pakati panu amene angaweruze mlandu pakati pa abale ake? 6 Kodi m’bale azitengera m’bale wake kukhoti, kwa anthu osakhulupirira?+
7 Kunena zoona, ndiye kuti mwalephereratu ngati mukutengerana kukhoti.+ Bwanji osangolola kulakwiridwa?+ Bwanji osalola kuberedwa?+ 8 M’malomwake, inuyo mumachita zolakwa ndiponso mumabera ena, ndipo abale anu ndi amene mumawachitira zimenezi.+
9 Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu?+ Musasocheretsedwe. Adama,+ opembedza mafano,+ achigololo,+ amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo,+ amuna ogona amuna anzawo,+ 10 akuba, aumbombo,+ zidakwa,+ olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.+ 11 Ndipo ena mwa inu munali otero.+ Koma mwasambitsidwa kukhala oyera,+ mwapatulidwa,+ mwayesedwa olungama+ m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu,+ komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.+
12 Zinthu zonse ndi zololeka kwa ine, koma si zonse zimene zili zaphindu.+ Zinthu zonse ndi zololeka+ kwa ine, koma sindidzalola kuti chinthu china chizindilamulira.+ 13 Chakudya ndi cha mimba, ndipo mimba ndi ya chakudya,+ koma Mulungu adzawononga mimba ndi chakudya chomwe.+ Choncho thupi silochitira dama koma ndi la Ambuye,+ ndipo Ambuye ndiye mwini thupi.+ 14 Koma Mulungu anaukitsa Ambuye+ kwa akufa+ ndipo adzaukitsanso ife mwa mphamvu yake.+
15 Kodi simukudziwa kuti matupi anu ndiwo ziwalo+ za Khristu?+ Ndiye kodi ine nditenge ziwalo za Khristu n’kuzisandutsa ziwalo za hule?+ Zosatheka zimenezo! 16 Kodi zoona inu simukudziwa kuti amene wadziphatika kwa hule amakhala thupi limodzi ndi hulelo? Pakuti anati, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+ 17 Koma amene waphatikana ndi Ambuye wakhala mzimu+ umodzi ndi iye.+ 18 Thawani dama.+ Tchimo lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita dama amachimwira thupi lake.+ 19 Kodi zoona inu simukudziwa kuti thupi lanu ndilo kachisi+ wa mzimu woyera umene uli mwa inu,+ umene munapatsidwa ndi Mulungu? Ndiponso mwiniwake wa inuyo si inu,+ 20 pakuti munagulidwa pa mtengo wokwera.+ Mulimonse mmene zingakhalire, lemekezani Mulungu+ ndi matupi anu.+
7 Tsopano pa nkhani imene munalemba ija, ndi bwino kuti mwamuna asakhudze+ mkazi. 2 Koma chifukwa cha kuwanda kwa dama,*+ mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake+ ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake. 3 Mwamuna azipereka kwa mkazi wake mangawa ake,+ mkazinso achite chimodzimodzi kwa mwamuna wake.+ 4 Mkazi asachite ulamuliro pathupi lake. Ulamulirowo ukhale ndi mwamuna wake.+ Mwamunanso asachite ulamuliro pathupi lake, koma ulamulirowo ukhale ndi mkazi wake.+ 5 Musamanane,+ kupatulapo ngati mwagwirizana kuimitsa kaye mangawawo kwa nthawi yodziwika,+ kuti muthere nthawi pa kupemphera, kenako mukhalenso mwa nthawi zonse, kuopera kuti Satana angapitirize kumakuyesani+ mukalephera kudzigwira.+ 6 Komabe, ndikunena zimenezi mokupatsani ufulu wozitsatira,+ osati mokulamulani.+ 7 Koma ndikanakonda amuna onse akanakhala ngati ineyo.+ Komabe, aliyense ali ndi mphatso+ yake yochokera kwa Mulungu. Wina m’njira iyi, winanso m’njira inayo.
8 Tsopano ndikunena kwa osakwatira+ ndi kwa akazi amasiye kuti, ndi bwino akhalebe mmene ineyo ndililimu.+ 9 Koma ngati sangathe kudziletsa,+ akwatire, pakuti ndi bwino kukwatira+ kusiyana ndi kuvutika ndi chilakolako.+
10 Kwa okwatira ndikupereka malangizo awa, kwenikweni osati ineyo koma Ambuye,+ kuti mkazi asasiye mwamuna wake,+ 11 koma ngati angamusiye, akhale choncho wosakwatiwa. Apo ayi, abwererane ndi mwamuna wakeyo. Mwamunanso asasiye mkazi wake.
12 Koma kwa enawa, ineyo, osati Ambuye,+ ndikunena kuti: Ngati pali m’bale amene ali ndi mkazi wosakhulupirira, ndipo mkaziyo akulola kukhala naye, asamusiye mkaziyo. 13 Ndiponso mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupirira, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye mwamuna wakeyo. 14 Pakuti mwamuna wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wake, ndiponso mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha m’baleyo, apo ayi, ana anu akanakhala osayera,+ koma tsopano ndi oyera.+ 15 Koma ngati wosakhulupirirayo wachoka,+ achoke. M’bale kapena mlongo sakhala womangika zinthu zikatero, koma Mulungu anakuitanani kuti mukhale mu mtendere.+ 16 Pakuti mkaziwe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mwamuna wako?+ Kapena mwamunawe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mkazi wako?+
17 Munthu aliyense akhale mmene Yehova wamugawira gawo lake,+ mmene Mulungu wamuitanira.+ Izi n’zimene ndikukhazikitsa+ m’mipingo yonse. 18 Kodi pali mwamuna amene anaitanidwa ali wodulidwa?+ Akhalebe wodulidwa. Alipo kodi amene anaitanidwa ali wosadulidwa?+ Asadulidwe.+ 19 Mdulidwe+ sutanthauza kalikonse, ndipo kusadulidwa+ sikutanthauza kanthu, koma kusunga malamulo a Mulungu ndiko kofunika.+ 20 Wina aliyense akhalebe+ mmene analili poitanidwa.+ 21 Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usade nazo nkhawa zimenezo,+ koma ngati ungathenso kumasuka, tengerapo mwayi pamenepo. 22 Pakuti aliyense amene ali mwa Ambuye amene anaitanidwa ali kapolo ndi womasulidwa wa Ambuye,+ momwemonso amene anaitanidwa ali mfulu+ ndi kapolo+ wa Khristu. 23 Munagulidwa pa mtengo wokwera,+ lekani kukhala akapolo+ a anthu. 24 Abale, wina aliyense akhalebe mmene analili+ poitanidwa, ndipo akhalebe pa ubwenzi ndi Mulungu.
25 Tsopano kunena za amene sali pabanja,* ndilibe lamulo lililonse la Ambuye, koma ndikupereka maganizo anga+ monga munthu amene ndinasonyezedwa chifundo ndi Ambuye+ kuti ndikhale wokhulupirika.+ 26 Chotero ndikuganiza kuti zingakhale bwino, malinga ndi mavuto amene tili nawo, kuti mwamuna akhalebe mmene alili.+ 27 Kodi ndiwe womangika kwa mkazi?+ Leka kufunafuna njira yomasukira.+ Kodi ndiwe womasuka kwa mkazi? Leka kufunafuna mkazi. 28 Koma ngakhale utakwatira, sikuti uchimwa.+ Ndipo ngati amene sali pabanja* walowa m’banja, sikuti wachimwa. Komabe, olowa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.+ Choncho ine ndikukutetezani.
29 Komanso abale dziwani izi: Nthawi yotsalayi yafupika.+ Choncho amene ali ndi akazi azikhala ngati alibe,+ 30 ndipo amene akulira azikhala ngati amene sakulira. Amene akusangalala azikhala ngati amene sakusangalala, ndipo amene amagula zinthu azikhala ngati opanda kanthu. 31 Amene amagwiritsira ntchito dzikoli+ azikhala ngati amene sakuligwiritsira ntchito mokwanira, pakuti zochitika za padzikoli zikusintha.+ 32 Ndithudi, ndikufuna kuti mukhale opanda nkhawa.+ Mwamuna wosakwatira amadera nkhawa zinthu za Ambuye, mmene angakondweretsere Ambuye. 33 Koma mwamuna wokwatira amadera nkhawa+ zinthu za dziko, mmene angakondweretsere mkazi wake,+ 34 ndipo amakhala wogawanika. Nayenso mkazi wosakwatiwa, komanso namwali, amadera nkhawa zinthu za Ambuye,+ kuti akhale woyera m’thupi lake ndi mu mzimu wake. Koma mkazi wokwatiwa amadera nkhawa zinthu za dziko, mmene angakondweretsere mwamuna wake.+ 35 Ndikunenatu zimenezi kuchitira ubwino wanu, osati kuti ndikuchititseni kukhala omangika, koma kuti ndikulimbikitseni kuchita choyenera+ ndiponso kutumikira Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.+
36 Koma ngati wina akuona kuti zikumuvuta kukhalabe yekha,*+ ngati wapitirira pachimake pa unyamata, ndipo ngati ziyenera kutero, achite mmene akufunira, sachimwa. Akwatire.+ 37 Koma ngati wina ndi wokhazikika mumtima mwake ndipo alibe chomuvutitsa, koma amatha kulamulira mtima wake, ndipo wasankha mumtima mwake kukhalabe wosakwatira,* wachita bwino.+ 38 Nayenso amene walekana ndi moyo wokhala yekha* n’kulowa m’banja wachita bwino,+ koma amene sanalowe m’banja wachita bwino koposa.+
39 Mkazi ndi womangika pa nthawi yonse imene mwamuna wake ali moyo.+ Komano mwamuna wake akamwalira, mkaziyo ndi womasuka kukwatiwa ndi aliyense amene akufuna, koma akwatiwe mwa Ambuye.+ 40 Komabe angakhale wosangalala kwambiri ngati apitiriza mmene alili.+ Ndi mmene ine ndikuonera. Ndipo ndine wotsimikiza mtima kuti ndilinso ndi mzimu wa Mulungu.+
8 Tsopano ponena za zakudya zoperekedwa kwa mafano,+ tikudziwa kuti tonse ndife odziwa zinthu.+ Kudziwa zinthu kumachititsa munthu kudzitukumula, koma chikondi chimamangirira.+ 2 Ngati wina akuganiza kuti akudziwa za chinachake,+ sanachidziwebe mokwanira.+ 3 Koma ngati munthu akukonda Mulungu,+ ameneyo amadziwika kwa Mulungu.+
4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+ 5 Pakuti ngakhale ilipo yotchedwa “milungu,”+ kaya kumwamba+ kapena padziko lapansi,+ ndipo n’zoona ilipodi “milungu” yambiri ndi “ambuye” ambiri,+ 6 kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi+ amene ndi Atate.+ Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye, ndipo ifeyo ndife ake.+ Ndipo pali Ambuye+ mmodzi, Yesu Khristu,+ amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo.
7 Ngakhale zili choncho, si onse amene amadziwa zimenezi.+ Koma ena, pokhala ozolowera mafano enaake mpaka panopo, akamadya chakudya choperekedwa kwa fano amachidya monga choperekedwadi kwa fano,+ ndipo popeza chikumbumtima chawo n’chofooka, chimaipitsidwa.+ 8 Koma chakudya sichingatikometse pamaso pa Mulungu.+ Ngati sitinadye chakudyacho, sikuti tamulakwira, ndiponso ngati tadya, sikuti tamukondweretsa mwapadera.+ 9 Koma muzikhalabe osamala kuti ufulu wanuwo usakhale chopunthwitsa kwa ofooka.+ 10 Pakuti ngati wina angaone iweyo wodziwa zinthuwe ukudya chakudya m’kachisi wa mafano, kodi chikumbumtima cha munthu wofooka uja sichidzamulimbikitsa kudya zakudya zoperekedwa kwa mafano?+ 11 Zikatero, ungawononge munthu wofookayo, yemwe ndi m’bale wako amene Khristu anamufera,+ chifukwa chakuti ukudziwa zinthu. 12 Koma inu mukamachimwira abale anu motero ndi kuvulaza chikumbumtima chawo+ chofookacho, mukuchimwira Khristu. 13 Chotero ngati chakudya chikukhumudwitsa+ m’bale wanga, sindidzadyanso nyama m’pang’ono pomwe, kuti ndisakhumudwitse m’bale wanga.+
9 Kodi sindine mfulu?+ Kodi sindine mtumwi?+ Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu?+ Kodi inu sindinu ntchito yanga mwa Ambuye? 2 Ngati sindine mtumwi kwa ena, mosakayikira ndine mtumwi kwa inu, popeza ndinu chidindo chotsimikizira+ utumwi wanga mwa Ambuye.
3 Yankho langa kwa amene amandikayikira ndi ili:+ 4 Tili ndi ufulu wa kudya+ ndi kumwa, si choncho kodi? 5 Tili ndi ufulu wotenga alongo amene ndi akazi athu+ pa maulendo, mmene amachitira atumwi ena onse ndiponso abale a Ambuye+ komanso Kefa,+ si choncho kodi? 6 Kapena kodi ine ndi Baranaba+ ndife tokha amene tilibe ufulu wosiya kugwira ntchito yakuthupi?+ 7 Alipo kodi msilikali amene amatumikira, koma n’kumadzilipira yekha? Ndani amalima munda wa mpesa koma osadya zipatso zake?+ Kapena ndani amaweta ziweto koma osamwako mkaka wake?+
8 Kodi ndikulankhula zinthu izi mwa nzeru za anthu?+ Kodi Chilamulo+ sichinenanso zinthu zimenezi? 9 Pakuti m’chilamulo cha Mose muli mawu akuti: “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+ Kodi ndi ng’ombe zimene Mulungu akusamalira? 10 Kapena kodi mawu amenewo kwenikweni akunenera ife? Ndithudi, mawu amenewo analembera ife,+ chifukwa wolima ayenera kulima ndi chiyembekezo ndipo munthu wopuntha mbewu azipuntha ndi chiyembekezo chodzadya nawo.+
11 Ngati tabzala zinthu zauzimu+ mwa inu, kodi ndi nkhani yaikulu ngati tikukolola zinthu zakuthupi mwa inu?+ 12 Ngati anthu ena amagwiritsa ntchito ufulu umenewu pa inu,+ kodi ife sitili oyenera kutero kuposa amenewo? Ngakhale zili choncho, sitinagwiritse ntchito ufulu umenewo,+ koma timadzichitira tokha zinthu zonse, kuti tisapereke chododometsa chilichonse ku uthenga wabwino+ wonena za Khristu. 13 Kodi simukudziwa kuti anthu ochita ntchito zopatulika amadya+ za m’kachisi, ndipo amene amatumikira+ kuguwa lansembe nthawi zonse amagawana gawo ndi guwa lansembe? 14 Momwemonso, Ambuye anakonza+ kuti olengeza uthenga wabwino azipeza zodzisamalira pa moyo kudzera mwa uthenga wabwino.+
15 Koma sindinagwiritse ntchito dongosolo lililonse loterolo.+ Ndiponso, sikuti ndalemba zimenezi kuti dongosolo limeneli liyambe kugwira ntchito kwa ine ayi, pakuti zingakhale bwino kuti ineyo ndife kusiyana ndi kuti . . . ndipo palibe munthu angatsutse chifukwa chimene ndikudzitamira!+ 16 Tsopano ngati ndikulengeza uthenga wabwino,+ chimenechi si chifukwa chodzitamira, pakuti ndinalamulidwa kutero.+ Ndithudi, tsoka+ kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino! 17 Ndikachita zimenezi mwaufulu,+ ndili ndi mphoto.+ Koma ndikachita motsutsana ndi kufuna kwanga, sindingachitire mwina, ndinebe woyang’anira mogwirizana ndi udindo+ umene unaikidwa m’manja mwanga. 18 Choncho mphoto yanga ndi chiyani? Ndi yakuti polengeza uthenga wabwino ndipereke uthengawo kwaulere,+ kuti ndisagwiritse ntchito molakwa ufulu wanga pa zinthu zokhudzana ndi uthenga wabwino.
19 Pakuti ngakhale ndine womasuka kwa anthu onse, ndadzipanga kapolo+ kwa onse, kuti ndipindule+ anthu ochuluka. 20 Motero kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda,+ kuti ndipindule Ayuda. Kwa anthu otsatira chilamulo+ ndinakhala ngati wotsatira chilamulo+ kuti ndipindule anthu otsatira chilamulo, ngakhale kuti sindili pansi pa chilamulo. 21 Kwa anthu opanda chilamulo+ ndinakhala ngati wopanda chilamulo,+ kuti ndipindule anthu opanda chilamulo. Ngakhale zili choncho, sikuti ndine wopanda chilamulo+ kwa Mulungu koma ndili pansi pa chilamulo kwa Khristu.+ 22 Kwa ofooka ndinakhala wofooka, kuti ndipindule ofooka.+ Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana,+ kuti mulimonse mmene zingakhalire ndipulumutseko ena. 23 Koma ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso+ kwa ena.
24 Kodi simukudziwa kuti ochita mpikisano wa liwiro+ amathamanga onse, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphoto?+ Thamangani+ m’njira yoti mukalandire mphotoyo.+ 25 Ndiponso, munthu aliyense wochita nawo mpikisano amakhala wodziletsa+ pa zinthu zonse. Iwo amachita zimenezo kuti apeze nkhata ya kumutu imene imawonongeka,+ koma ife, kuti tikapeze nkhata ya kumutu yosakhoza kuwonongeka.+ 26 Motero, sikuti ndikungothamanga+ osadziwa kumene ndikulowera. Mmene ndikuponyera nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi,+ 27 koma ndikumenya thupi langa+ ndi kulitsogolera ngati kapolo, kuopera kuti, pambuyo poti ndalalikira kwa ena, ineyo ndingakhale wosayenera+ m’njira inayake.
10 Tsopano sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale, kuti makolo athu akale, onse anali pansi pa mtambo+ ndipo onse anawoloka nyanja.+ 2 Onse anabatizidwa mwa Mose,+ kudzera mwa mtambo ndi mwa nyanja. 3 Ndiponso, onse anadya chakudya chimodzimodzi chauzimu,+ 4 ndipo onse anamwa chakumwa chimodzimodzi chauzimu.+ Pakuti anali kumwa pathanthwe lauzimu+ limene linali kuwatsatira, ndipo thanthwelo+ linatanthauza Khristu.+ 5 Ngakhale zinali choncho, ambiri a iwo Mulungu sanakondwere+ nawo, ndipo anathana+ nawo m’chipululu.
6 Tsopano zinthu zimenezi zinakhala zitsanzo kwa ife, kuti ifenso tisakhale anthu olakalaka zinthu zoipa+ ngati mmene iwo anachitira. 7 Ndipo tisapembedze mafano, mmene ena mwa iwo anachitira,+ monga mmene Malemba amanenera kuti: “Anthu anakhala pansi ndi kudya ndiponso kumwa. Kenako anaimirira n’kuyamba kusangalala.”+ 8 Tisamachite dama,+ mmene ena mwa iwo anachitira dama, n’kufa 23,000 tsiku limodzi.+ 9 Kapena tisamuyese Yehova,+ mmene ena mwa iwo anamuyesera,+ n’kuwonongeka polumidwa ndi njoka.+ 10 Tisakhalenso ong’ung’udza, mmene ena mwa iwo anang’ung’udzira,+ wowonongayo+ n’kuwawononga onsewo. 11 Tsopano zinthu zimenezi zinali kuwagwera monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze+ ifeyo amene mapeto a nthawi* zino atifikira.+
12 N’chifukwa chake amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.+ 13 Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene amagwera anthu ena.+ Koma Mulungu ndi wokhulupirika+ ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire,+ koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira+ kuti muthe kuwapirira.
14 Ndiye chifukwa chake, okondedwa anga, thawani+ kupembedza mafano.+ 15 Ndikulankhula nanu ngati anthu ozindikira.+ Dziwani nokha zimene ndikunena. 16 Kodi kapu+ ya dalitso imene timadalitsa, sitanthauza kugawana magazi a Khristu?+ Kodi mkate umene timanyema,+ sutanthauza kugawana thupi la Khristu? 17 Popeza pali mkate umodzi, ifeyo, ngakhale kuti tilipo ambiri,+ ndife thupi limodzi,+ pakuti tonse tikudya nawo mkate umodziwo.+
18 Taganizirani zochitika za Isiraeli wakuthupi:+ Kodi amene amadyako zoperekedwa nsembe sindiye kuti akugawana ndi guwa lansembe?+ 19 Ndiye ndinene chiyani? Kuti choperekedwa nsembe kwa fano chili kanthu, kapena kuti fanolo ndi kanthu?+ 20 Ayi, koma ndikunena kuti zinthu zimene mitundu ina imapereka nsembe imazipereka kwa ziwanda,+ osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti mukhale ogawana ndi ziwanda.+ 21 Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova*+ komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya “patebulo la Yehova”+ komanso patebulo la ziwanda. 22 Kapena “kodi tikufuna kuputa nsanje+ ya Yehova”? Kodi mphamvu zathu zingafanane ndi zake?+
23 Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu.+ Zinthu zonse ndi zololeka,+ koma si zonse zimene zili zolimbikitsa.+ 24 Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi,+ koma zopindulitsanso wina.+
25 Chilichonse chogulitsidwa pamsika wa nyama muzidya+ popanda kufunsa mafunso, poopera chikumbumtima+ chanu, 26 chifukwa “dziko lapansi ndi zonse za mmenemo+ ndi za Yehova.”+ 27 Ngati wina mwa osakhulupirira wakuitanani ndipo mwapita, kadyeni zonse zimene wakupatsani,+ popanda kufunsa mafunso poopera chikumbumtima chanu.+ 28 Koma wina akakuuzani kuti: “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo poopera amene wakuuzaniyo ndiponso poopera chikumbumtima.+ 29 Sindikunena “chikumbumtima” chako koma cha munthu winayo. N’chifukwa chiyani ufulu wanga ukulamulidwa ndi chikumbumtima cha munthu wina?+ 30 Ngati ndikudya chakudyacho nditayamika Mulungu, kodi ndinyozedwe pa chinthu chimene ndayamikira?+
31 Ndiye chifukwa chake, kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.+ 32 Pewani kukhala okhumudwitsa+ kwa Ayuda, ngakhalenso kwa Agiriki, ndi kwa mpingo wa Mulungu, 33 monga mmene ineyo ndikukondweretsera anthu onse m’zinthu zonse.+ Sikuti ndikungofuna zopindulitsa ine ndekha ayi,+ koma zopindulitsa anthu ambiri, kuti apulumutsidwe.+
11 Muzitsanzira ine, monga mmene inenso ndimatsanzirira Khristu.+
2 Tsopano ndikukuyamikirani chifukwa chakuti mukundikumbukira m’zinthu zonse, ndipo mukusunga miyambo+ monga mmene ndinaiperekera kwa inu. 3 Koma ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.+ Mutu wa mkazi ndi mwamuna,+ ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.+ 4 Mwamuna aliyense amene akupemphera kapena kunenera atavala chinachake kumutu akuchititsa manyazi mutu wake,+ 5 koma mkazi aliyense amene akupemphera kapena kunenera+ osavala kanthu kumutu akuchititsa manyazi mutu wake,+ popeza n’chimodzimodzi ndi kumeta mpala.+ 6 Ngati mkazi savala kanthu kumutu, amete mpala, koma ngati zili zochititsa manyazi kuti mkazi amete kwambiri tsitsi lake kapena amete mpala,+ azivala chakumutu.+
7 Mwamuna sayenera kuphimba kumutu kwake, popeza iye ndi chifaniziro+ ndi ulemerero+ wa Mulungu, koma mkazi ndi ulemerero wa mwamuna.+ 8 Pakuti mwamuna sanachokere kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna,+ 9 ndiponso mwamuna sanalengedwere mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna.+ 10 Ndiye chifukwa chake mkazi ayenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro kumutu kwake+ chifukwa cha angelo.+
11 Ndiponso mwa Ambuye, mkazi sakhalapo popanda mwamuna kapena mwamuna popanda mkazi.+ 12 Pakuti monga mkazi ali wochokera kwa mwamuna,+ mwamunanso amakhalapo kudzera mwa mkazi,+ koma zinthu zonse ndi zochokera kwa Mulungu.+ 13 Weruzani nokha: Kodi n’koyenera mkazi kupemphera kwa Mulungu osaphimba kumutu? 14 Kodi chikhalidwe sichikuphunzitsani kuti ngati mwamuna ali ndi tsitsi lalitali, zimenezi n’zochititsa manyazi kwa iye, 15 koma ngati mkazi ali ndi tsitsi lalitali, ndi ulemerero kwa iye?+ Zili choncho chifukwa wapatsidwa tsitsi lakelo m’malo mwa chovala kumutu.+ 16 Komabe, ngati alipo wina amene akuoneka kuti akutsutsa+ zimenezi pofuna chikhalidwe china,+ ifeyo, monganso mipingo ya Mulungu, tilibe chikhalidwe chinanso.
17 Koma pamene ndikupereka malangizo awa, sikuti ndikukuyamikirani ayi, chifukwa mukasonkhana pamodzi, simusonkhanira zabwino, koma zoipa.+ 18 Choyamba, mukasonkhana mumpingo, ndamva kuti pamachitika magawano pakati panu,+ ndipo m’mbali zina ndikukhulupirira kuti zimenezi ndi zoona. 19 Pakuti payeneradi kukhala magulu ampatuko+ pakati panu, kuti anthu ovomerezedwa aonekere pakati panu.+
20 Chotero, mukasonkhana pamalo amodzi, sizitheka kudya chakudya chamadzulo cha Ambuye moyenerera.+ 21 Pakuti, mukamadya, aliyense amakhala atadya chakudya chake chamadzulo, choncho wina amakhala ndi njala koma wina amakhala woledzera. 22 Zoona, kodi mulibe nyumba zimene mungadyeremo ndi kumweramo?+ Kapena kodi mukunyoza mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi anthu amene alibe kalikonse?+ Kodi ndinene chiyani kwa inu? Ndikuyamikireni? Koma pa izi zokha sindingakuyamikireni.
23 Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye n’zimene inenso ndinakupatsirani, zakuti Ambuye Yesu, usiku+ umene anali kukaperekedwa anatenga mkate. 24 Ndipo atayamika, anaunyemanyema+ n’kunena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+ 25 Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu+ atadya chakudya chamadzulo, ndipo anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano+ pamaziko a magazi anga.+ Muzichita zimenezi nthawi zonse pamene mukumwa za m’kapu imeneyi pondikumbukira.”+ 26 Pakuti nthawi zonse+ pamene mukudya mkate umenewu ndi kumwa za m’kapu imeneyi, mukulengezabe imfa+ ya Ambuye, mpaka iye adzafike.+
27 Ndiye chifukwa chake aliyense wakudya mkatewu kapena kumwa za m’kapu ya Ambuye mosayenerera, adzakhala ndi mlandu+ wokhudza thupi ndi magazi+ a Ambuye. 28 Munthu ayambe wadzifufuza+ ngati ali woyenerera kudya mkatewu ndi kumwa za m’kapuyi. 29 Pakuti munthu wakudya ndi kumwa, akudya ndi kumwa chilango+ chake ngati sazindikira thupilo. 30 Ndiye chifukwa chake ambiri mwa inu ali ofooka ndi odwaladwala, ndipo angapo akugona+ mu imfa. 31 Koma ngati tingazindikire mmene tilili, sitingaweruzidwe.+ 32 Komabe tikaweruzidwa,+ ndiye kuti taphunzitsidwa ndi Yehova+ kuti tisalandire chilango+ pamodzi ndi dziko.+ 33 Choncho abale anga, mukasonkhana pamodzi kuti mudye chakudya chamadzulo cha Ambuye,+ dikiranani. 34 Ngati wina ali ndi njala, adye kunyumba,+ kuti musasonkhanire kuweruzidwa.+ Koma nkhani zotsalazo ndidzathana nazo ndikadzafika komweko.
12 Tsopano abale, ponena za mphatso zauzimu,+ sindikufuna kuti mukhale osadziwa. 2 Mukudziwa kuti pamene munali a mitundu ina,+ munali kutsogoleredwa m’njira zosiyanasiyana ku mafano+ osalankhula.+ 3 Choncho ndikufuna mudziwe kuti palibe wolankhula mwa mzimu wa Mulungu amene anganene kuti: “Yesu ndi wotembereredwa!”+ Palibenso amene anganene popanda mzimu woyera kuti: “Yesu ndiye Ambuye!”+
4 Tsopano mphatso zilipo zamitundumitundu,+ koma mzimu ndi umodzi,+ 5 ndipo pali mautumiki osiyanasiyana,+ koma Ambuye ndi mmodzi.+ 6 Palinso ntchito zosiyanasiyana,+ koma Mulungu amene amachita ntchito zonsezo mwa anthu onse+ ndi mmodzi.+ 7 Tsopano ntchito za mzimu zimapatsidwa kwa munthu aliyense pa cholinga chopindulitsa.+ 8 Mwachitsanzo, mwa mzimu wina amapatsidwa mawu anzeru,+ ndipo wina amapatsidwa mawu ozindikira+ mwa mzimu womwewo. 9 Mwa mzimu womwewonso wina amapatsidwa chikhulupiriro,+ wina mphatso za kuchiritsa.+ 10 Winanso amapatsidwa mphatso yochita ntchito zamphamvu,+ wina kunenera,+ wina kuzindikira+ mawu ouziridwa,+ wina kulankhula malilime osiyanasiyana,+ ndiponso wina kumasulira+ malilime. 11 Koma ntchito zonsezi, mzimu umodzimodziwo+ ndiwo umazichita, pogawira+ aliyense payekha malinga ndi chifuniro cha mzimuwo.+
12 Pakuti mofanana ndi thupi lomwe ndi limodzi koma lili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonse za thupi, ngakhale ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi,+ ndi mmenenso Khristu alili.+ 13 Pakuti ndi mzimu umodzi, tonsefe tinabatizidwa+ kukhala thupi limodzi, kaya tikhale Ayuda kapena Agiriki, akapolo kapena mfulu, ndipo tonsefe tinamwetsedwa+ mzimu umodzi.
14 Ndithudi, thupi si chiwalo chimodzi, koma zambiri.+ 15 Ngati phazi linganene kuti: “Popeza sindine dzanja, sindili mbali ya thupi,” chimenecho si chifukwa chopangitsa phazi kusakhala mbali ya thupi.+ 16 Ndipo ngati khutu linganene kuti: “Popeza sindine diso, sindili mbali ya thupi,” chimenecho si chifukwa chopangitsa khutu kusakhala mbali ya thupi.+ 17 Thupi lonse likanakhala diso, kodi mphamvu ya kumva ikanakhala kuti? Thupi lonse likanakhala khutu, kodi bwenzi tikumanunkhiza ndi chiyani? 18 Koma Mulungu anaika ziwalo m’thupi, chilichonse m’malo ake, mmene iye anafunira.+
19 Zonsezo zikanakhala chiwalo chimodzi,+ nanga thupi likanakhala kuti? 20 M’malomwake, ziwalozo n’zambiri,+ koma thupi ndi limodzi. 21 Diso silingauze dzanja kuti: “Ndilibe nawe ntchito,” kapenanso, mutu sungauze mapazi kuti: “Ndilibe nanu ntchito.” 22 Koma ziwalo za thupi zimene zimaoneka ngati zofooka+ ndizo zofunika. 23 Ndipo mbali za thupi zimene timaziona ngati zosalemekezeka kwambiri, n’zimene timazipatsa ulemu wochuluka,+ chotero mbali zathu zosaoneka bwino zimaoneka bwino kwambiri, 24 pamene mbali zathu zooneka bwino kale sizifunikira kalikonse. Ngakhale zili choncho, Mulungu analumikiza bwino thupi lonse, kuika ulemu wochuluka pa mbali imene inalibe ulemuwo, 25 kuti thupi lisakhale logawanika, koma ziwalo zake zisamalirane mofanana.+ 26 Ndipo chiwalo chimodzi chikavutika, ziwalo zina zonse zimavutikira nacho limodzi,+ komanso chiwalo chimodzi chikalemekezedwa,+ ziwalo zina zonse zimasangalalira nacho limodzi.+
27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.+ 28 Mulungu waika ziwalo zosiyanasiyana mumpingo.+ Choyamba atumwi,+ chachiwiri aneneri,+ chachitatu aphunzitsi,+ kenako ntchito zamphamvu,+ mphatso za kuchiritsa,+ utumiki wothandiza anthu,+ luso loyendetsa zinthu,+ ndi malilime osiyanasiyana.+ 29 Sikuti onse angakhale atumwi, angatero ngati? Sikuti onse angakhale aneneri, angatero ngati? Sikuti onse angakhale aphunzitsi, angatero ngati? Si onse amachita ntchito zamphamvu, ndi onse ngati? 30 Si onse amene ali ndi mphatso za kuchiritsa, ndi onse ngati? Si onse amalankhula malilime,+ ndi onse ngati? Sikuti onse ndi omasulira,+ ndi onse ngati? 31 M’malomwake, pitirizani kufunafuna mwachangu mphatso zazikulu.+ Komabe, ine ndikuonetsani njira yopambana.+
13 Ngati ndimalankhula malilime+ a anthu ndi a angelo koma ndilibe chikondi, ndakhala ngati belu longolira, kapena chinganga chosokosera.+ 2 Ndipo ngati ndili ndi mphatso yonenera,+ yodziwa zinsinsi zonse zopatulika,+ yodziwa zinthu zonse,+ komanso ngati ndili ndi chikhulupiriro chonse choti n’kusuntha nacho mapiri,+ koma ndilibe chikondi, sindili kanthu.+ 3 Ngati ndapereka zanga zonse kudyetsa ena,+ ndipo ngati ndapereka thupi langa+ kuti ndidzitame, koma ndilibe chikondi,+ sindinapindule m’pang’ono pomwe.
4 Chikondi+ n’choleza mtima+ ndiponso n’chokoma mtima.+ Chikondi sichichita nsanje,+ sichidzitama,+ sichidzikuza,+ 5 sichichita zosayenera,+ sichisamala zofuna zake zokha,+ sichikwiya.+ Sichisunga zifukwa.+ 6 Sichikondwera ndi zosalungama,+ koma chimakondwera ndi choonadi.+ 7 Chimakwirira zinthu zonse,+ chimakhulupirira zinthu zonse,+ chimayembekezera zinthu zonse,+ chimapirira zinthu zonse.+
8 Chikondi sichitha.+ Koma kaya pali mphatso za kunenera, zidzatha. Kaya kulankhula malilime, kudzatha. Ngakhale mphatso ya kudziwa zinthu, idzatha.+ 9 Pakuti tikudziwa+ moperewera ndipo tikunenera mopereweranso.+ 10 Koma chokwanira chikadzafika,+ choperewerachi chidzatha. 11 Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, ndiponso kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula,+ ndasiya zachibwana. 12 Pakuti pa nthawi ino sitikuona bwinobwino chifukwa tikugwiritsa ntchito galasi losaoneka bwinobwino,+ koma pa nthawiyo zidzakhala maso ndi maso.+ Pa nthawi ino zimene ndikudziwa n’zoperewera, koma pa nthawiyo ndidzadziwa bwinobwino ngati mmene ineyo ndikudziwikira bwinobwino.+ 13 Komabe, tsopano patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.+
14 Yesetsani kukhala ndi chikondi, komanso pitirizani kufunafuna mwachangu mphatso zauzimu,+ makamaka kunenera.+ 2 Chifukwa wolankhula lilime lachilendo salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu, pakuti palibe amene amamva zonena zake,+ koma amalankhula zinsinsi zopatulika+ mwa mzimu. 3 Komabe, wonenera amathandiza+ anthu ndipo amawalimbikitsa ndi kuwatonthoza ndi mawu ake. 4 Wolankhula lilime lachilendo amadzilimbikitsa yekha, koma wonenera amalimbikitsa mpingo. 5 Tsopano ndikanakonda kuti nonsenu muzilankhula malilime,+ koma ndikuona kuti ndi bwino kuti muzinenera.+ Ndithudi, wonenera amaposa wolankhula malilime achilendo,+ kupatulapo ngati wa malilimeyo amasulira, kuti amange mpingo. 6 Koma pa nthawi ino abale, ngati ineyo ndingabwere kwa inu ndikulankhula malilime, kodi mungapindulepo chiyani ngati sindingakulankhuleni ndi mawu amene ndalandira kuchokera kwa Mulungu,+ kapena ndi mphatso yodziwa zinthu,+ kapena ndi ulosi, kapena ndi chiphunzitso?
7 Chabwino, zinthu zopanda moyo zimamveka kulira kwake,+ kaya chikhale chitoliro kapena zeze. Koma ngati maliridwe ake angokhala amodzi osasinthasintha, kodi n’zotheka kudziwa nyimbo imene ikuimbidwa ndi chitoliro kapena zezeyo? 8 Ndithudi, ngati lipenga likulira mwa mamvekedwe osadziwika bwino, ndani angakonzekere nkhondo?+ 9 Momwemonso, ngati simukulankhula zomveka ndi lilime lanu,+ zingatheke bwanji kudziwa zimene mukunena? Kwenikweni mudzakhala mukulankhula kwa mphepo.+ 10 Pangakhale zinenero zosiyanasiyana padziko lapansi, koma palibe zinenero zimene zilibe tanthauzo. 11 Chotero ngati sindikudziwa tanthauzo la chinenero, ndimakhala mlendo+ kwa wolankhulayo, ndipo wolankhulayo amakhala mlendo kwa ine. 12 Inunso chimodzimodzi, popeza mukufunitsitsa mphatso za mzimu.+ Chotero, yesetsani kukhala nazo zochuluka kuti mumange mpingo.+
13 Choncho amene amalankhula lilime lachilendo apemphere kuti athe kumasulira.+ 14 Pakuti ngati ndikupemphera m’lilime lachilendo, mphatso yanga ya mzimu ndi imene ikupemphera,+ koma maganizo anga amakhala opanda phindu. 15 Ndiye chofunika n’chiyani? Ndipemphere ndi mphatso ya mzimu, koma ndipempherenso ndi maganizo anga. Ndiimbe chitamando ndi mphatso ya mzimu,+ koma ndiimbenso ndi maganizo anga.+ 16 Chifukwa ngati mupereka chitamando ndi mphatso ya mzimu, kodi munthu wamba anganene bwanji “Ame”+ pa kuyamika kwanu, posadziwa zimene mukunena? 17 Zoonadi, mukupereka chiyamiko m’njira yabwino, koma munthu winayo sakulimbikitsidwa.+ 18 Ndimayamika Mulungu kuti ndimalankhula malilime ambiri kuposa nonsenu.+ 19 Ngakhale zili choncho, ndi bwino kuti mumpingo ndilankhule mawu asanu omveka, kutinso ndilangize ena ndi mawuwo, kusiyana n’kulankhula mawu 10,000 m’lilime lachilendo.+
20 Abale, musakhale ana aang’ono pa luntha la kuzindikira,+ koma khalani tiana pa zoipa,+ ndipo pa luntha la kuzindikira khalani aakulu msinkhu.+ 21 M’Chilamulo muli mawu akuti: “‘Anthu awa+ ndidzawalankhula m’malilime a alendo,+ ndipo ndidzawalankhula ndi milomo ya anthu achilendo, koma iwo sadzandimverabe,’ watero Yehova.”+ 22 Chotero malilimewo ndi chizindikiro+ kwa osakhulupirira,+ osati kwa okhulupirira, koma kunenera ndi kwa okhulupirira,+ osati osakhulupirira. 23 Ndiye chifukwa chake, ngati mpingo wonse wasonkhana malo amodzi ndipo onse akulankhula malilime,+ ndiyeno mwalowa anthu osadziwa kalikonse kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti ndinu amisala? 24 Koma ngati nonse mukunenera, ndiyeno mwalowa winawake wosakhulupirira kapena munthu wamba, iye amadzudzulidwa ndi nonsenu.+ Nonsenu mumamufufuza mosamala. 25 Zobisika za mumtima mwake zimaululika,+ moti adzagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi, n’kulambira Mulungu, ndi kunena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.”+
26 Ndiyeno zizikhala bwanji, abale? Mukasonkhana pamodzi, wina amakhala ndi salimo, wina chiphunzitso, wina mawu amene walandira kuchokera kwa Mulungu, wina lilime lachilendo, wina kumasulira.+ Zochitika zonse zikhale zolimbikitsa.+ 27 Ndipo ngati pali anthu olankhula lilime lachilendo, asapose awiri kapena atatu, azisiyirana mpata, ndipo wina amasulire.+ 28 Koma ngati palibe womasulira, wa malilimeyo akhale chete mumpingo. Adzilankhule yekha mumtima+ ndipo alankhule kwa Mulungu. 29 Aneneri awiri kapena atatu+ alankhule, ndipo ena onse azindikire tanthauzo la zimene iwo alankhula.+ 30 Koma ngati mneneri wina amene wakhala pansi walandira mawu kuchokera kwa Mulungu,+ woyambayo akhale chete. 31 Pakuti nonse munganenere,+ koma mmodzi ndi mmodzi, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa.+ 32 Ndipo mphatso za mzimu za aneneri ziyenera kulamulidwa ndi aneneri. 33 Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo,+ koma wamtendere.+
Mofanana ndi m’mipingo yonse ya oyerawo, 34 akazi akhale chete+ m’mipingo, pakuti sikololeka kuti iwo azilankhula, koma akhale ogonjera,+ monga Chilamulo+ chimanenera. 35 Koma ngati akufuna kumvetsa chinachake, akafunse amuna awo kunyumba, popeza n’zochititsa manyazi+ kuti mkazi azilankhula mumpingo.
36 Kodi mawu a Mulungu anachokera kwa inu,+ kapena anafika kwa inu nokha?
37 Ngati munthu akuganiza kuti ndi mneneri kapena ali ndi mphatso ya mzimu, avomereze zimene ndakulemberanizi, chifukwa ndizo lamulo la Ambuye.+ 38 Koma ngati wina savomereza, akhale. 39 Choncho abale anga, pitirizani kufunafuna mwakhama uneneri,+ komanso musaletse kulankhula malilime.+ 40 Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.+
15 Tsopano abale, ndikukuuzani uthenga wabwino+ umene ndinaulengeza kwa inu,+ umenenso munaulandira, ndiponso umene mwakhazikikamo.+ 2 Mukupulumutsidwa+ ndi uthenga wabwino umenewo ngati mwaugwiritsitsa. Popanda kutero, ndiye kuti munakhala okhulupirira pachabe,+ malinga ndi mawu amene ndinakuuzani polengeza uthengawo kwa inu.
3 Mwa zinthu zofunika kwambiri zimene ndinakupatsirani zija, zimenenso ineyo ndinalandira,+ panali zonena kuti, Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba.+ 4 Ndiponso kuti anaikidwa m’manda,+ kenako anaukitsidwa+ tsiku lachitatu,+ mogwirizana ndi Malemba.+ 5 Panalinso zoti anaonekera kwa Kefa,+ kenako kwa atumwi 12+ aja. 6 Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero,+ koma ena anagona mu imfa. 7 Kenako anaonekera kwa Yakobo,+ kenakonso kwa atumwi onse.+ 8 Koma pomalizira pake anaonekera kwa ine,+ ngati khanda lobadwa masiku asanakwane.
9 Ineyo ndine wamng’ono kwambiri+ mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza+ mpingo wa Mulungu. 10 Koma mwa kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu, ndili monga ndililimu. Ndipo kukoma mtima kwake kwakukulu kumene anandisonyeza sikunapite pachabe,+ koma ndinagwira ntchito molimbika kuposa atumwi ena onse.+ Ngakhale zili choncho, si mwa ine ndekha ayi, koma kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kumene kuli nane.+ 11 Komabe, kaya ndi ineyo kapena iwowo, zimene tikulalikira ndi zomwezo, zimenenso mwazikhulupirirazo.+
12 Tsopano ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa,+ bwanji ena mwa inu akunena kuti akufa sadzaukitsidwa?+ 13 Chifukwa ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanauke.+ 14 Koma ngati Khristu sanauke, kulalikira kwathu n’kopanda pake, ndipo chikhulupiriro chathu n’chopanda pake.+ 15 Ndiponso, ndiye kuti ifenso takhala mboni zonama za Mulungu,+ chifukwa tachita umboni+ wonamizira Mulungu kuti anaukitsa Khristu+ pamene sanamuukitse, ngati akufa sadzaukadi.+ 16 Pakuti ngati akufa sadzauka, Khristunso sanauke. 17 Ndipo ngati Khristu sanauke, chikhulupiriro chanu chilibe ntchito ndipo mukadali m’machimo anu.+ 18 Ndiye kutinso anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu,+ kutha kwawo kunali komweko.+ 19 Ngati tayembekezera Khristu+ m’moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.
20 Komabe, Khristu anaukitsidwa kwa akufa,+ n’kukhala chipatso choyambirira+ cha amene akugona mu imfa.+ 21 Popeza imfa+ inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka+ kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi. 22 Pakuti monga mwa Adamu onse akufa,+ momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa+ moyo. 23 Koma aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira,+ kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo*+ kwake. 24 Ndiyeno pa mapeto pake, adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake, atathetsa maboma onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse.+ 25 Pakuti ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi+ ake. 26 Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.+ 27 Pakuti Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Koma pamene akunena kuti ‘waika zinthu zonse pansi pake,’+ n’zodziwikiratu kuti sakuphatikizapo amene anaika zinthu zonsezo pansi pa iye.+ 28 Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake,+ Mwanayonso adzadziika pansi pa amene+ anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.+
29 Apo ayi, kodi amene akubatizidwa kuti akhale akufa adzatani?+ Ngati akufa sadzauka,+ n’chifukwa chiyani anthuwo akubatizidwa+ kuti akhale akufa? 30 Kodi ifeyo tikuikiranji moyo wathu pachiswe nthawi zonse?+ 31 Tsiku ndi tsiku ndimakhala pa ngozi yoti ndikhoza kufa.+ Ndikukutsimikizirani zimenezi ndili wokondwera nanu,+ abale, kukondwera kumene ndili nako mwa Khristu Yesu Ambuye wathu. 32 Ngati ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso+ monga ena anachitira, ndinapindulapo chiyani? Ngati akufa sadzauka, “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”+ 33 Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.+ 34 Dzukani ku tulo tanu+ kuti mukhale olungama ndipo musamachite tchimo, pakuti ena sadziwa Mulungu.+ Ndikulankhula zimenezi kuti muchite manyazi.+
35 Ngakhale zili choncho, wina anganene kuti: “Kodi akufa adzaukitsidwa motani? Inde, kodi iwo adzauka ndi thupi lotani?”+ 36 Wopusa iwe! Chimene wabzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitafa kaye.+ 37 Ndipo chimene wafesa si mmera umene umakulawo, koma mbewu chabe,+ kaya ya tirigu kapena ina iliyonse. 38 Koma Mulungu amaipatsa thupi+ monga mwa kufuna kwake,+ ndipo mbewu iliyonse amaipatsa thupi lake. 39 Mnofu sukhala wa mtundu umodzi, koma pali mnofu wa munthu, ndipo pali wa nyama, palinso wa mbalame, ndi winanso wa nsomba.+ 40 Palinso matupi akumwamba,+ ndi matupi+ apadziko lapansi, koma ulemerero+ wa matupi akumwamba ndi wina, ndipo ulemerero wa matupi apadziko lapansi ndi winanso. 41 Ulemerero wa dzuwa+ ndi wosiyana ndi ulemerero wa mwezi,+ ndipo ulemerero wa nyenyezi ndi winanso. Ngakhale ulemerero wa nyenyezi+ ina, umasiyana ndi ulemerero wa inzake.
42 Ndi mmenenso zilili ndi kuuka kwa akufa.+ Thupi limafesedwa lili lokhoza kuwonongeka, limaukitsidwa losakhoza kuwonongeka.+ 43 Limafesedwa lonyozeka,+ limaukitsidwa mu ulemerero.+ Limafesedwa lofooka,+ limaukitsidwa mu mphamvu.+ 44 Limafesedwa thupi lanyama,+ limaukitsidwa thupi lauzimu.+ Ngati pali thupi lanyama, palinso lauzimu. 45 Zinachita kulembedwa kuti: “Munthu woyambirira, Adamu, anakhala munthu wamoyo.”+ Adamu womalizira anakhala mzimu+ wopatsa moyo.+ 46 Ngakhale zili choncho, choyambacho si chauzimu ayi koma chamnofu. Kenako panabwera chauzimu.+ 47 Munthu woyambayo anachokera padziko lapansi ndipo anapangidwa ndi fumbi.+ Wachiwiriyo anachokera kumwamba.+ 48 Mmene wopangidwa ndi fumbiyo alili,+ ndi mmenenso opangidwa ndi fumbiwo alili. Ndipo mmene wakumwambayo alili,+ ndi mmenenso akumwambawo alili.+ 49 Ndiponso, monga tilili m’chifaniziro+ cha wopangidwa ndi fumbi uja, tidzakhalanso m’chifaniziro+ cha wakumwambayo.
50 Koma abale, ndikunenetsa kuti mnofu ndi magazi sizingalowe ufumu wa Mulungu.+ Komanso chowonongeka sichingalandire kusawonongeka.+ 51 Tamverani! Ndikukuuzani chinsinsi chopatulika: Si tonse amene tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasandulika,+ 52 m’kamphindi, m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza. Pakuti lipengalo+ lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osakhoza kuwonongeka, ndipo tidzasandulika. 53 Pakuti chokhoza kuwonongekachi chidzavala kusawonongeka,+ ndipo chokhoza kufachi+ chidzavala kusafa. 54 Koma chokhoza kuwonongekachi chikadzavala kusawonongeka, ndipo chokhoza kufachi chikadzavala kusafa, pamenepo adzakwaniritsidwa mawu amene analembedwa kuti: “Imfa+ yamezedwa kwamuyaya.”+ 55 “Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?”+ 56 Mphamvu+ imene imabala imfa ndiyo uchimo, koma mphamvu ya uchimo ndi Chilamulo.+ 57 Koma Mulungu ayamikike, pakuti amatithandiza kuti tipambane kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+
58 Choncho abale anga okondedwa, khalani olimba,+ osasunthika, okhala ndi zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye,+ podziwa kuti zonse zimene mukuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.+
16 Tsopano ponena za chopereka+ chopita kwa oyerawo,+ inunso tsatirani malangizo amene ndinapereka ku mipingo ya ku Galatiya.+ 2 Tsiku lililonse loyamba la mlungu, aliyense wa inu aziika kenakake pambali kunyumba kwake malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wake, kuti ndikadzafika, zopereka zisadzaperekedwe pa nthawi imeneyo. 3 Koma ndikadzafika kumeneko, amuna alionse amene mungawavomereze m’makalata,+ ndidzawatuma kuti adzapititse mphatso yanu yachifundoyo ku Yerusalemu. 4 Komabe, ngati kudzakhala kofunika kuti inenso ndidzapite, tidzapitira limodzi.
5 Ndidzafika kwa inu pochokera ku Makedoniya, pakuti ndipita ku Makedoniya.+ 6 Mwina ndidzakhala nanu pang’ono kumeneko, ngakhalenso kwa nyengo yonse yachisanu, kuti mudzandiperekeze+ kumene ndizidzapitako. 7 Pakuti sindikufuna kukuonani panopo mongodutsa chabe, koma ndikufuna kuti ndidzakhale nanu kanthawi ndithu,+ ngati Yehova+ alola.+ 8 Koma ndikhalabe kuno ku Efeso+ mpaka chikondwerero cha Pentekosite, 9 pakuti khomo lalikulu la mwayi wautumiki landitsegukira,+ koma pali otsutsa ambiri.
10 Komabe, Timoteyo+ akadzafika mudzaonetsetse kuti asadzakhale ndi mantha pakati panu, pakuti iye akuchita ntchito ya Yehova,+ mmenenso ine ndikuchitira. 11 Choncho pasadzapezeke munthu womuderera.+ Mudzamuperekeze mu mtendere kuti adzafike kwa ine kunoko, pakuti ineyo ndikumuyembekezera pamodzi ndi abale.
12 Tsopano kunena za m’bale wathu Apolo,+ ndinamuchonderera kwambiri kuti abwere kwanuko pamodzi ndi abale, koma iye sanafune kubwera pa nthawi ino. Adzabwera akadzapeza mpata.
13 Khalani maso,+ limbani m’chikhulupiriro,+ pitirizani kuchita chamuna,+ khalani amphamvu.+ 14 Zonse zimene mukuchita, muzichite mwachikondi.+
15 Tsopano ndikukulimbikitsani mokudandaulirani, abale, kuti: Mukudziwa kuti banja la Sitefana ndilo chipatso choyambirira+ mu Akaya ndi kuti anadzipereka kutumikira oyera.+ 16 Inunso pitirizani kudzipereka kwa anthu ngati amenewo, ndi kwa aliyense wogwirizana nafe pa ntchitoyi, ndiponso wogwira ntchito molimbika.+ 17 Koma ndikusangalala kuti Sitefana+ ndi Fotunato ndi Akayiko ali kuno ndi ine, pakuti alowa m’malo mwanu. 18 Pakuti atsitsimutsa mtima wanga+ ndi wanunso. Chotero, anthu otere muziwalemekeza.+
19 Mipingo ya ku Asia ikupereka moni.+ Akula ndi Purisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m’nyumba mwawo,+ akupereka moni wochokera pansi pa mtima kwa inu nonse, mwa Ambuye. 20 Abale onse akukupatsani moni. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kopatulika.+
21 Tsopano landirani moni wanga wolemba ndekha ndi dzanja langa, ineyo Paulo.+
22 Ngati wina aliyense sakonda Ambuye, atembereredwe.+ Inde, idzani Ambuye!+ 23 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu kukhale nanu. 24 Nonsenu landirani chikondi changa mwa Khristu Yesu.
Onani Zakumapeto 9.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “munthu wakuthupi.”
Mawu ake enieni, “anthu akuthupi.”
Mawu ake enieni, “anthu akuthupi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 7.
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.
Onani Zakumapeto 7.
Mawu ake enieni, “anamwali.”
Mawu ake enieni, “namwali.”
Mawu ake enieni, “kusungabe unamwali wake.”
Mawu ake enieni, “kusunga unamwali wake.”
Onani mawu a m’munsi pavesi 36.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 8.