Kwa Aroma
1 Ndine Paulo kapolo+ wa Yesu Khristu, woitanidwa+ kuti ndikhale mtumwi,+ ndiponso wosankhidwa kuti ndilalikire uthenga wabwino wa Mulungu.+ 2 Uthenga umenewu anaulonjeza kalekale kudzera mwa aneneri+ ake m’Malemba oyera. 3 Uthengawo umanena za Mwana wake, amene anatuluka m’mbewu ya Davide+ monga munthu,+ 4 koma amene Mulungu mwa mphamvu+ yake anam’lengeza kukhala Mwana wake+ mwa mzimu woyera+ pomuukitsa kwa akufa.+ Ameneyu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu. 5 Kudzera mwa iyeyu, tinalandira kukoma mtima+ kwakukulu ndiponso ndinasankhidwa kukhala mtumwi+ kuti mitundu yonse ikhale yomvera mwa chikhulupiriro+ chifukwa cha dzina lake. 6 Pakati pa mitundu imeneyo palinso inuyo amene munaitanidwa kuti mukhale ake a Yesu Khristu. 7 Ndikulembera inu nonse amene muli ku Roma monga okondedwa a Mulungu, oitanidwa+ kukhala oyera:+
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere+ wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu+ zikhale ndi inu.
8 Choyamba, ndikuyamika+ Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, pakuti chikhulupiriro chanu chikusimbidwa+ m’dziko lonse. 9 Mulungu, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika ndi moyo wanga wonse polalikira uthenga wabwino wonena za Mwana wake, ndiye mboni yanga+ ya mmene ndimakutchulirani m’mapemphero anga nthawi zonse.+ 10 Ndimamupempha kuti ngati n’kotheka mwa chifuniro+ chake, ulendo uno wokha ndibwere kwanuko. 11 Popeza ndikulakalaka kukuonani+ kuti ndikugawireni mphatso+ inayake yauzimu kuti mukhale olimba, 12 kapena kuti tidzalimbikitsane+ mwa chikhulupiriro, chanu ndi changa.+
13 Koma sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale,+ kuti nthawi zambiri ndinkafuna kubwera kwanuko,+ koma pakhala zondilepheretsa mpaka pano. Ndikufuna kuti ndidzapeze zipatso+ pakati pa inu monganso ndinachitira pakati pa mitundu ina yonse. 14 Ineyo ndili ndi ngongole kwa Agiriki, kwa anthu amene si Agiriki, kwa anthu anzeru+ ndi kwa opusa. 15 Chotero ndikufunitsitsa kudzalengeza uthenga wabwino+ kwa inunso kumeneko ku Roma.+ 16 Pakuti sindichita nawo manyazi+ uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndi mphamvu+ ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro,+ choyamba kwa Myuda+ kenako kwa Mgiriki.+ 17 Mu uthenga wabwinowu, chilungamo+ cha Mulungu chimaululidwa chifukwa cha chikhulupiriro cha munthu.+ Zikatero, chikhulupiriro cha munthuyo chimalimbanso monga mmene Malemba amanenera kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.”+
18 Mkwiyo wa Mulungu+ ukusonyezedwa kuchokera kumwamba pa anthu onse osaopa Mulungu ndi ochita zosalungama+ amene akupondereza choonadi+ m’njira yosalungama.+ 19 Chifukwa chake n’chakuti, zimene anthu angathe kudziwa ponena za Mulungu zikuonekera pakati pawo,+ popeza Mulungu anazisonyeza kwa iwo.+ 20 Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo,+ makhalidwe a Mulungu osaoneka+ ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu+ wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga+ moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.+ 21 Chifukwa chakuti, ngakhale anam’dziwa Mulungu, iwo sanam’patse ulemerero monga Mulungu kapena kumuyamikira.+ M’malomwake anayamba kulingalira zinthu zopanda pake+ ndipo mtima wawo wopusawo unachita mdima.+ 22 Ngakhale anali kunena motsimikiza kuti ndi anzeru, iwo anakhala opusa+ 23 ndipo anasandutsa ulemerero+ wa Mulungu amene sawonongeka kukhala ngati chifaniziro+ cha munthu, mbalame, zolengedwa za miyendo inayi ndi zokwawa,+ zonsezo zimene zimawonongeka.
24 Chotero malinga ndi zilakolako za m’mitima mwawo, Mulungu anawasiya kuti achite zonyansa,+ kuti matupi awo+ achitidwe chipongwe.+ 25 Anateronso kwa anthu amene anasinthanitsa choonadi+ cha Mulungu ndi bodza+ polambira chilengedwe ndi kuchichitira utumiki wopatulika m’malo mochita zimenezo kwa Iye amene anazilenga, amene ndi wotamandika kosatha. Ame. 26 Ndiye chifukwa chake Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zamanyazi za kugonana,+ popeza akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo n’kumachita zosemphana ndi chibadwa.+ 27 Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi+ n’kumatenthetsana okhaokha mwachiwawa m’chilakolako choipa, amuna ndi amuna anzawo,+ kuchitirana zonyansa+ ndi kulandiriratu mphoto+ yoyenerera kulakwa kwawo.+
28 Ndiponso monga mmene iwo sanafunire kumudziwa Mulungu molondola,+ iye anawasiya ndi maganizo awo oipa,+ kuti azichita zinthu zosayenerazo,+ 29 popeza anadzazidwa ndi zosalungama+ zonse, kuipa+ konse, kusirira konse kwa nsanje,+ ndi uchimo+ wonse. Mtima wawo unadzala kaduka,+ umbanda,+ ndewu,+ chinyengo+ ndi njiru.+ Anakonda manong’onong’o+ 30 ndi miseche.+ Anakhala odana ndi Mulungu, achipongwe,+ odzikweza,+ odzimva,+ oyambitsa zoipa,+ osamvera makolo,+ 31 osazindikira,+ osasunga mapangano,+ opanda chikondi chachibadwa+ ndiponso opanda chifundo.+ 32 Amenewa ngakhale kuti amalidziwa bwino lamulo lolungama la Mulungu,+ lakuti amene amachita zinthu zimenezi n’ngoyenera imfa,+ iwo amapitiriza kuzichita. Kuwonjezera apo, amagwirizananso+ ndi anthu amene amachita zimenezo.
2 Choncho munthu iwe,+ kaya ukhale ndani, ulibe chifukwa chomveka chodzilungamitsira ngati umaweruza ena.+ Pakuti pa nkhani imene ukuweruza nayo wina, ukudzitsutsa wekha, chifukwa iwenso woweruzawe+ umachita zomwezo.+ 2 Tikudziwa kuti Mulungu amaweruza anthu amene amachita zimenezi kuti ndi oyenera kulandira chilango ndipo chiweruzo chake ndi chogwirizana ndi choonadi.+
3 Koma tsopano, iwe+ amene umaweruza anthu amene amachita zinthu zimene iwenso umachita, kodi ukuganiza kuti udzazemba chiweruzo cha Mulungu?+ 4 Kapena kodi ukunyoza kukoma mtima kwake kwakukulu,+ kusakwiya msanga+ kwake ndi kuleza mtima kwake,+ chifukwa chakuti sudziwa kuti cholinga cha kukoma mtima kwa Mulungu ndicho kukuthandiza kuti ulape?+ 5 Koma chifukwa chakuti ndiwe wosafuna kusintha khalidwe+ ndiponso wa mtima wosalapa,+ ukudzisungira mkwiyo wa Mulungu.+ Mulungu adzasonyeza mkwiyo+ umenewu pa tsiku loulula+ chiweruzo chake cholungama.+ 6 Iye adzaweruza aliyense malinga ndi ntchito zake motere:+ 7 Moyo wosatha kwa anthu amene popirira m’ntchito yabwino akuyesetsa kupeza ulemerero, ulemu ndi moyo wosakhoza kuwonongeka.+ 8 Koma adzapereka chilango ndi mkwiyo+ kwa okonda mikangano+ amenenso samvera choonadi+ koma amamvera zosalungama. 9 Aliyense wochita zoipa, kuyambira Myuda+ mpaka Mgiriki,+ adzaona nsautso ndi zowawa. 10 Koma aliyense wochita zabwino,+ choyamba Myuda+ kenako Mgiriki,+ adzalandira ulemerero, ulemu ndi mtendere. 11 Pakuti Mulungu alibe tsankho.+
12 Mwachitsanzo, onse amene anachimwa popanda chilamulo adzawonongekanso popanda chilamulo.+ Koma onse amene anachimwa ali ndi chilamulo+ adzaweruzidwa ndi chilamulo.+ 13 Pajatu akumva chabe chilamulo si amene amakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma otsatira+ chilamulo ndiwo adzayesedwa olungama.+ 14 Nthawi zonse anthu a mitundu+ amene alibe chilamulo+ akamachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo,+ amakhala chilamulo kwa iwo eni ngakhale kuti alibe chilamulo. 15 Amenewa ndiwo amasonyeza kuti mfundo za m’chilamulo zinalembedwa m’mitima mwawo,+ pamene chikumbumtima chawo+ chimachitira umboni pamodzi ndi iwowo, ndipo maganizo awo amawatsutsa+ ngakhalenso kuwavomereza. 16 Zimenezi zidzaonekera pa tsiku limene Mulungu, kudzera mwa Khristu Yesu, adzaweruze+ zinthu zobisika+ za anthu,+ mogwirizana ndi uthenga wabwino umene ndikulengeza.+
17 Tsopano ngati ndiwe Myuda dzina lokha+ ndipo umadalira chilamulo+ ndi kunyadira Mulungu,+ 18 umadziwa chifuniro chake,+ umakondwera ndi zinthu zapamwamba kwambiri chifukwa chakuti unaphunzitsidwa Chilamulo ndi mawu a pakamwa,+ 19 komanso uli wotsimikiza kuti ndiwe wotsogolera akhungu,+ muuni wa anthu amene ali mu mdima,+ 20 wowongolera anthu opanda nzeru,+ wophunzitsa tiana,+ womvetsa+ zinthu zofunika kuzidziwa ndi choonadi+ zopezeka m’Chilamulo . . . 21 kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha?+ Iwe amene umalalikira kuti “Usabe,”+ umabanso kodi?+ 22 Iwe amene umanena kuti “Usachite chigololo,”+ kodi umachitanso chigololo? Iweyo amene umalankhula zosonyeza kuti umanyansidwa ndi mafano, umabanso+ za mu akachisi kodi? 23 Iwe wonyadira chilamulo, kodi umachitiranso Mulungu chipongwe mwa kuphwanya Chilamulo?+ 24 Pakuti “dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu chifukwa cha inu”+ monga mmene Malemba amanenera.
25 Pajatu mdulidwe+ ndi waphindu pokhapokha ngati iweyo umatsatiradi chilamulo.+ Koma ngati umaphwanya chilamulo, ndiye kuti mdulidwe+ wako ndi wopanda tanthauzo.+ 26 Chotero ngati munthu wosadulidwa+ akusunga miyezo yolungama+ ya m’Chilamulo, kusadulidwa kwake kudzaonedwa ngati kudulidwa, kodi si choncho?+ 27 Munthu amene mwachibadwa ndi wosadulidwa, mwa kutsatira Chilamulo adzakuweruza iwe.+ Adzakuweruza iweyo amene umaphwanya malamulo, amene uli ndi malamulo olembedwa ndiponso ndiwe wodulidwa. 28 Pakuti iye amene ali Myuda kunja kokha si Myuda ayi,+ ndiponso mdulidwe wakunja kokha wochitidwa pathupi, si mdulidwe ayi.+ 29 Koma Myuda ndi amene ali wotero mkati,+ ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo satamandidwa+ ndi anthu koma ndi Mulungu.+
3 Choncho, kodi Myuda+ ndi woposa ena motani? Kapena kodi phindu la mdulidwe n’chiyani?+ 2 Iye amaposadi ena kwambiri m’njira iliyonse. Choyamba, chifukwa chakuti mawu opatulika a Mulungu+ anaikidwa m’manja mwa Ayuda. 3 Nanga ngati ena sanasonyeze chikhulupiriro,+ kodi chifukwa chakuti alibe chikhulupiriro+ ndiye kuti kukhala wokhulupirika kwa Mulungu n’kopanda pake?+ 4 Ayi! Koma Mulungu akhale wonena zoona,+ ngakhale kuti munthu aliyense angapezeke kukhala wonama,+ monganso Malemba amanenera kuti: “Mukamalankhula mumalankhula zachilungamo, kuti mupambane pamene mukuweruzidwa.”+ 5 Komabe, ngati kulungama kwa Mulungu+ kukuonekera chifukwa cha kusalungama kwathu, ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tingati Mulungu ndi wosalungama+ poonetsa mkwiyo wake? (Ndikulankhula mmene anthu+ amalankhulira.) 6 Ayi! Chifukwa Mulungu akapanda kutero, kodi dziko adzaliweruza motani?+
7 Tsopano ngati chifukwa cha bodza langa choonadi cha Mulungu+ chaonekera kwambiri, ndipo zimenezo zamubweretsera ulemerero, n’chifukwa chiyaninso ndikuweruzidwabe kukhala wochimwa?+ 8 Ndilekeranji kunena zimene amatinamizira zija,+ ndiponso zimene ena amati timanena zakuti: “Tiyeni tichite zoipa kuti pakhale zinthu zabwino”?+ Chiweruzo+ chowafikira anthu amenewo n’chogwirizana ndi chilungamo.+
9 Ndiye zikatero? Kodi tili pabwino kuposa ena?+ Ayi! Pakuti tanena kale poyamba paja kuti onse, Ayuda ndi Agiriki, ndi ochimwa+ 10 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Palibe munthu wolungama ndi mmodzi yemwe.+ 11 Palibe amene ali wozindikira ngakhale pang’ono, palibiretu amene akuyesetsa kupeza Mulungu.+ 12 Anthu onse apanduka, onse pamodzi akhala opanda pake. Palibe amene akusonyeza kukoma mtima, palibiretu ndi mmodzi yemwe.”+ 13 “Mmero wawo ndi manda otseguka. Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.”+ “M’milomo yawo muli poizoni wa njoka.”+ 14 “Ndipo m’kamwa mwawo mwadzaza mawu otukwana ndi opweteka.”+ 15 “Mapazi awo amathamangira kukhetsa magazi.”+ 16 “Kusakaza ndi kusautsa kuli m’njira zawo,+ 17 ndipo sadziwa njira ya mtendere.”+ 18 “Maso awo saona chifukwa choopera Mulungu.”+
19 Tikudziwa kuti zinthu zonse zimene Chilamulo+ chimanena chimazinena kwa amene ali m’Chilamulo, kuti pakamwa paliponse patsekedwe+ ndipo dziko lonse likhale loyenera+ kulandira chilango cha Mulungu.+ 20 Chotero pamaso pake palibe munthu amene adzayesedwe wolungama+ mwa ntchito za chilamulo,+ popeza chilamulo chimachititsa kuti tidziwe uchimo molondola.+
21 Koma tsopano, zaonekera kuti munthu akhoza kukhala wolungama kwa Mulungu+ popanda kutsatira Chilamulo. Zimenezi zinatchulidwanso+ m’Chilamulo+ ndi m’Zolemba za aneneri.+ 22 Kuoneka wolungama pamaso pa Mulungu kumeneku kungatheke mwa kukhulupirira Yesu Khristu,+ ndipo ndi kotheka kwa onse okhala ndi chikhulupiriro.+ Popeza palibe kusiyanitsa.+ 23 Pakuti onse ndi ochimwa+ ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.+ 24 Ndiponso, kuyesedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo+ lolipiridwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulere.+ 25 Mulungu anam’pereka monga nsembe yachiyanjanitso,+ mwa kukhala ndi chikhulupiriro m’magazi ake.+ Mulungu anachita izi pofuna kuonetsa chilungamo chake pokhululuka machimo+ amene anachitika kale, pamene iye anali kusonyeza khalidwe losakwiya msanga,+ 26 ndipo akuonetsa chilungamo chake+ m’nyengo inoyo pakutcha munthu amene ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu kuti ndi wolungama.+
27 Chotero, kodi pamenepa palinso chifukwa chodzitama nacho?+ Palibiretu. Malinga ndi chilamulo chiti?+ Chija chofuna ntchito?+ Ndithudi ayi, koma mwa lamulo la chikhulupiriro.+ 28 Popeza tsopano taona kuti munthu amayesedwa wolungama mwa chikhulupiriro, osati mwa ntchito za chilamulo.+ 29 Kapena kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha?+ Kodi salinso Mulungu wa anthu a mitundu ina?+ Inde, iye alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina,+ 30 ngati Mulungu alidi mmodzi.+ Iye ndi amene adzayese anthu odulidwa+ kuti ndi olungama chifukwa cha chikhulupiriro, ndiponso anthu osadulidwa+ adzawayesa olungama mwa chikhulupiriro chawo. 31 Koma kodi tikuthetsa chilamulo mwa chikhulupiriro chathu?+ Ayi! M’malomwake, tikulimbikitsa chilamulo.+
4 Popeza zili choncho, kodi tinene chiyani za Abulahamu kholo lathu?+ 2 Mwachitsanzo, chikhala kuti Abulahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito,+ akanakhala ndi chifukwa chodzitamandira, koma osati kwa Mulungu. 3 Kodi lemba limati chiyani paja? Limati: “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama.”+ 4 Chifukwa munthu amene wagwira ntchito+ saona malipiro ake ngati kukoma mtima kwakukulu,+ koma ngati ngongole.+ 5 Munthu amene sadalira ntchito zake koma amakhulupirira+ Mulungu, amayesedwa wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake,+ pakuti Mulungu amatha kuona munthu wosatsatira malamulo ake kukhala wolungama. 6 Davide ananena kuti munthu amene Mulungu amamuyesa wolungama popanda munthuyo kuchita ntchito ndi wodala. Iye anati: 7 “Odala ndi amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo+ ndipo machimo awo aphimbidwa.+ 8 Wodala ndi munthu amene Yehova sadzawerengera tchimo lake.”+
9 Chotero, kodi anthu odulidwa okha ndi amene amakhala odala choncho? Kapena kodi osadulidwa nawonso amakhala odala?+ Popeza timati: “Abulahamu anaonedwa ngati wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+ 10 Koma kodi iye anali wotani pamene anayesedwa wotero? Kodi anali wodulidwa kapena wosadulidwa?+ Sanali wodulidwa, koma wosadulidwa. 11 Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe monga chizindikiro.+ Chizindikiro chimenechi chinali chosonyeza kuti, chifukwa cha chikhulupiriro, Mulungu anamuyesa wolungama asanadulidwe, kuti adzakhale tate+ wa onse osadulidwa okhala ndi chikhulupiriro,+ kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama. 12 Kutinso adzakhale tate wa ana odulidwa, osati wa okhawo ochita mdulidwe, komanso wa amene amayenda moyenerera m’mapazi a chikhulupiriro chimene bambo wathu+ Abulahamu anali nacho asanadulidwe.
13 Pakuti Abulahamu kapena mbewu yake sanalonjezedwe kuti adzalandira dziko monga cholowa chawo chifukwa cha chilamulo ayi.+ Analandira lonjezolo chifukwa chakuti anali wolungama mwa chikhulupiriro.+ 14 Chifukwa ngati anthu oumirira kusunga chilamulo ndiwo adzalandire cholowacho, ndiye kuti chikhulupiriro chilibenso ntchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa.+ 15 Kwenikweni, Chilamulo chimabala mkwiyo,+ koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.+
16 Chotero iye anapatsidwa lonjezolo+ chifukwa cha chikhulupiriro, kuti likhale mwa kukoma mtima kwakukulu,+ ndiponso kuti likhale lotsimikizika kwa mbewu yake yonse,+ osati yotsatira Chilamulo yokha ayi, komanso yotsatira chikhulupiriro cha Abulahamu. (Iye ndiye tate+ wa ife tonse, 17 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Ndakuika kuti ukhale tate wa mitundu yambiri.”)+ Izi zinali choncho pamaso pa Uyo amene Abulahamu anam’khulupirira, inde pamaso pa Mulungu, amene amapereka moyo kwa akufa+ ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.+ 18 Anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro+ chakuti adzakhala tate wa mitundu yambiri,+ ngakhale kuti zimenezi zinkaoneka kuti n’zosatheka. Anakhulupirira zimenezi mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ 19 Ndiponso, ngakhale kuti chikhulupiriro chake sichinafooke, anaganizira za thupi lake, limene linali lakufa tsopano,+ popeza anali ndi zaka pafupifupi 100.+ Anaganiziranso zakuti Sara anali wosabereka.+ 20 Koma chifukwa cha lonjezo+ la Mulungu, iye sanagwedezeke pa chikhulupiriro chake+ ndipo chikhulupiriro chakecho chinamulimbitsa.+ Mwa kutero, anapereka ulemerero kwa Mulungu 21 ndipo anali wotsimikiza kuti zimene Mulungu analonjeza anali ndi mphamvu yozichita.+ 22 Ndiye chifukwa chake “anaonedwa ngati wolungama.”+
23 Komabe, zonena kuti “anayesedwa+ wolungama” sizinalembedwere iye yekha,+ 24 komanso ife amene tidzayesedwa otero, chifukwa chakuti timakhulupirira iye amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu kwa akufa.+ 25 Iye anaperekedwa chifukwa cha machimo athu+ ndipo anaukitsidwa kuti tiyesedwe olungama.+
5 Chotero, popeza tsopano tayesedwa olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro,+ tiyeni tikhale pa mtendere+ ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 2 Mwa ameneyunso, ndiponso chifukwa cha chikhulupiriro, takhala ndi ufulu wolowa+ m’kukoma mtima kwakukulu, mmene tilimo tsopano. Ndipo tiyeni tikondwere chifukwa cha chiyembekezo+ cha ulemerero wa Mulungu. 3 Si zokhazo, koma tiyeni tikondwere pamene tili m’masautso,+ popeza tikudziwa kuti chisautso chimabala chipiriro.+ 4 Chipiriro chimachititsa kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu.+ Kukhala ovomerezeka kwa Mulungu kumabala chiyembekezo,+ 5 ndipo chiyembekezocho sichitikhumudwitsa+ chifukwa Mulungu wadzaza chikondi chake+ m’mitima yathu+ kudzera mwa mzimu woyera+ umene tinapatsidwa.
6 Popeza pamene tinali ofooka,+ Khristu anafera anthu osapembedza Mulungu pa nthawi yoikidwiratu.+ 7 Pakuti n’chapatali kuti munthu wina afere munthu wolungama.+ Zoonadi, mwina wina angalimbe mtima kufera+ munthu wabwino.+ 8 Koma Mulungu akuonetsa chikondi chake+ kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.+ 9 Tsopano adzachita zoposa pamenepo mwa kutipulumutsa ku mkwiyo wake+ kudzera mwa Khristu, popeza tayesedwa olungama kudzera m’magazi a Khristuyo.+ 10 Pakuti ngati pamene tinali adani,+ tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake,+ nanji tsopano pamene tayanjanitsidwa, tidzapulumutsidwa ndithu ndi moyo wake.+ 11 Ndipo si zokhazo, koma tikukondweranso mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene tayanjanitsidwa ndi Mulungu kudzera mwa iye.+
12 Ndiye chifukwa chake monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi,+ ndi imfa+ kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa+ . . . 13 Paja Chilamulo chisanabwere, uchimo unalimo kale m’dziko, koma munthu saimbidwa mlandu wa kuchimwa pamene palibe lamulo.+ 14 Ngakhale zili choncho, imfa inalamulira monga mfumu kuyambira kwa Adamu mpaka kwa Mose,+ ngakhalenso kwa anthu amene sanachimwe monga mmene anachimwira Adamu,+ yemwe ndi wolingana ndi iye amene anali kubwera.+
15 Koma mmene zilili ndi mphatsoyi si mmene zinalili ndi uchimowo. Popeza ngati mwa uchimo wa munthu mmodzi ambiri anafa, kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere zinasefukira kwa anthu ambiri.+ Mphatso yaulere imeneyi inaperekedwa limodzi ndi kukoma mtima kwakukulu kudzera mwa munthu mmodzi,+ Yesu Khristu. 16 Ndiponso, mmene zilili ndi mphatso yaulereyi+ zasiyana ndi mmene zinthu zinachitikira kudzera mwa munthu mmodzi amene anachimwa.+ Pakuti chiweruzo+ chimene chinatsatira tchimo limodzi lija chinabweretsa uchimo kwa onse,+ koma mphatso imene inatsatira machimo ambiri, inachititsa kuti anthu atchedwe olungama.+ 17 Ngati chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo+ imfa inalamulira monga mfumu+ kudzera mwa munthuyo, amene alandira kukoma mtima kwakukulu+ kochuluka ndiponso mphatso yaulere+ yaikuluyo ya chilungamo, adzakhala ndi moyo ndi kulamulira monga mafumu+ kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.+
18 Chotero, mmene zinakhalira kuti mwa uchimo umodzi anthu kaya akhale amtundu wotani anaweruzidwa kukhala ochimwa,+ momwemonso mwa kuchita chinthu chimodzi cholungamitsa,+ anthu kaya akhale amtundu wotani+ akuyesedwa olungama kuti akhale ndi moyo.+ 19 Pakuti monga mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo, ambiri+ anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera+ kwa munthu mmodziyu, ambiri+ adzakhala olungama.+ 20 Chilamulo+ chinalowapo kuti kuchimwa kuonekere kuti ndi kwakukulu.+ Koma pamene uchimo+ unawonjezeka, kukoma mtima kwakukulu+ kunasefukiranso. 21 Chifukwa chiyani? Kuti mmene uchimo unalamulira monga mfumu pamodzi ndi imfa,+ momwemonso kukoma mtima kwakukulu+ kulamulire monga mfumu kudzera m’chilungamo. Zimenezi zichitike kuti moyo wosatha+ ubwere kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.
6 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tipitirize kuchimwa kuti kukoma mtima kwakukulu kuwonjezeke?+ 2 Tisatero ayi! Popeza kuti tinafa ku uchimo,+ kodi tipitirize kuchimwa chifukwa chiyani?+ 3 Kapena simudziwa kuti tonsefe amene tinabatizidwa ndipo tsopano tili mu mgwirizano ndi Khristu Yesu+ tinabatizidwanso mu imfa yake?+ 4 Motero tinaikidwa m’manda+ pamodzi ndi iye pobatizidwa mu imfa yake, kuti monga mmene Khristu anaukitsidwira kwa akufa mwa ulemerero wa Atate,+ ifenso tiziyenda m’moyo watsopano.+ 5 Chifukwa ngati tagwirizana naye pokhala ndi imfa yofanana ndi yake,+ ndithudi tidzagwirizananso naye poukitsidwa mofanana ndi iye.+ 6 Pakuti tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi iye pamtengo,+ kuti thupi lathu lauchimo likhale ngati lakufa,+ kuti tisapitirize kukhala akapolo a uchimo.+ 7 Chifukwa munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.+
8 Ndiponso, ngati tinafadi limodzi ndi Khristu, timakhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo limodzi ndi iye.+ 9 Tikudziwa kuti pamene tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa,+ sadzafanso.+ Imfa sikuchitanso ufumu pa iye. 10 Popeza imfa imene anafa, anafa kuti achotse uchimo kamodzi kokha basi,+ koma moyo umene ali nawo, akukhala nawo kuti azichita chifuniro cha Mulungu.+ 11 Momwemonso inuyo dzioneni ngati akufa+ ku uchimo koma amoyo+ kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
12 Choncho musalole kuti uchimo uzilamulirabe monga mfumu+ m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zawo.+ 13 Ndipo musapereke ziwalo zanu ku uchimo+ kuti zikhale zida zochitira zinthu zosalungama,+ koma dziperekeni kwa Mulungu monga anthu amene auka kwa akufa.+ Ziwalo zanunso muzipereke kwa Mulungu monga zida+ zochitira chilungamo. 14 Uchimo usakhale mbuye kwa inu, chifukwa simuli pansi pa chilamulo+ koma pansi pa kukoma mtima kwakukulu.+
15 Ndiye zikatero? Kodi tichite tchimo chifukwa chakuti sitili m’chilamulo+ koma m’kukoma mtima kwakukulu?+ Tisayese n’komwe kutero! 16 Kodi simukudziwa kuti ngati mudziperekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvera, mumakhala akapolo ake chifukwa chakuti mumamumvera,+ kaya mukhale akapolo a uchimo+ umene umatsogolera ku imfa,+ kapena mukhale akapolo a kumvera+ kumene kumatsogolera ku chilungamo?+ 17 Koma tikuyamika Mulungu kuti ngakhale poyamba munali akapolo a uchimo, munamvera mochokera pansi pa mtima mtundu wa chiphunzitso chimene chinaperekedwa kwa inu.+ 18 Inde, popeza munamasulidwa+ ku uchimo, munakhala akapolo+ a chilungamo.+ 19 Ndikulankhulatu monga munthu chifukwa cha kufooka kwa matupi anu.+ Pakuti mmene munaperekera ziwalo zanu+ kuti zikhale akapolo a zonyansa+ ndiponso akapolo a kusamvera malamulo ndi cholinga chakuti muzichita zinthu zophwanya malamulo, perekaninso ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a chilungamo kuti muzichita ntchito za chiyero.+ 20 Popeza pamene munali akapolo a uchimo,+ munali omasuka ku chilungamo.
21 Kodi pa nthawiyo munali kukhala ndi zipatso zotani?+ Zinali zinthu+ zimene tsopano mumachita nazo manyazi. Ndipo pothera pake pa zinthu zimenezo ndi imfa.+ 22 Koma tsopano chifukwa munamasulidwa ku uchimo ndipo munakhala akapolo a Mulungu,+ mukukhala ndi zipatso+ za chiyero, ndipo pa mapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha.+ 23 Chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa,+ koma mphatso+ imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha+ kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+
7 Kodi mwina simukudziwa abale, (popeza ndikulankhula ndi anthu odziwa chilamulo,) kuti Chilamulo chimakhala mbuye wa munthu pamene munthuyo ali moyo?+ 2 Mwachitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi amamasuka ku lamulo la mwamuna wake.+ 3 Ngati angakwatiwe ndi mwamuna wina, mwamuna wake ali moyo, mkaziyo adzatchedwa wachigololo.+ Koma ngati mwamuna wake wamwalira, mkaziyo wamasuka ku lamulo lake, chotero si wachigololo ngati atakwatiwa ndi mwamuna wina.+
4 Choncho abale anga, thupi la Khristu linakupangani kukhala akufa ku Chilamulo,+ kuti mukhale a winawake,+ a iye amene anaukitsidwa kwa akufa,+ kuti tibale zipatso+ kwa Mulungu. 5 Chifukwa pamene tinali kukhala mogwirizana ndi thupi,+ zilakolako za uchimo zimene zinaonekera chifukwa cha Chilamulo zinali kugwira ntchito m’ziwalo zathu kuti tibale zipatso za imfa.+ 6 Koma tsopano tamasulidwa ku Chilamulo,+ chifukwa tafa+ ku chilamulo chimene chinali kutimanga chija, kuti tikhale akapolo+ m’njira yatsopano motsogoleredwa ndi mzimu,+ osati m’njira yakale motsogoleredwa ndi malamulo olembedwa.+
7 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Chilamulo ndi uchimo?+ Ayi m’pang’ono pomwe! Kunena zoona, sindikanadziwa uchimo+ zikanakhala kuti panalibe Chilamulo. Ndiponso, mwachitsanzo, sindikanadziwa kusirira kwa nsanje+ zikanakhala kuti Chilamulo sichinanene kuti: “Usasirire mwansanje.”+ 8 Koma chifukwa cha lamulo,+ uchimo unapeza njira yondichititsa kukhala wosirira chinthu chilichonse mwansanje. Chifukwa popanda chilamulo, uchimo unali wakufa.+ 9 Ndinalitu wamoyo chilamulo chisanabwere.+ Koma pamene malamulo anafika,+ uchimo unakhalanso ndi moyo, koma ineyo ndinafa.+ 10 Tsopano ine ndinaona lamulo lopatsa moyolo+ kuti ndi lobweretsa imfa.+ 11 Pakuti chifukwa cha lamulo, uchimo unapeza njira yondinyenga+ ndipo unandipha. 12 Choncho, Chilamulo kumbali yake n’choyera,+ ndipo malamulo ndi oyera, olungama+ ndi abwino.+
13 Ndiye kodi chinthu chabwino chinakhala imfa kwa ine? Ayi ndithu! Koma uchimo ndiwo unakhala imfa kwa ine, kuti uonekere kuti ndi umene ukubala imfa mwa ine kudzera m’chinthu chabwinocho,+ kuti kudzera m’malamulo, uchimowo uonekere kuti ndi woipa kwambiri.+ 14 Pakuti tikudziwa kuti Chilamulo n’chauzimu,+ koma ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo.+ 15 Sindimvetsetsa kuti n’chifukwa chiyani ndimachita zinthu motere. Chifukwa zimene ndimafuna kuchita, sindizichita. Koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimachita. 16 Komabe, ngati zimene sindifuna kuchita ndi zimene ndimachita,+ ndikuvomereza kuti Chilamulo ndi chabwino.+ 17 Koma tsopano amene akuchita zimenezo si inenso ayi, koma uchimo umene uli mwa ine.+ 18 Ndikudziwa kuti mwa ine, ndikunenatu za m’thupi langa, simukhala kanthu kabwino.+ Pakuti ndimafuna+ kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.+ 19 Chinthu chabwino chimene ndimafuna kuchita sindichita,+ koma choipa chimene sindifuna kuchita ndi chimene ndimachita. 20 Tsopano ngati zimene sindifuna ndi zimene ndikuchita, amene akuchita zimenezo si inenso ayi, koma uchimo umene ukukhala mwa ine.+
21 Chotero kwa ine, ndimapeza lamulo ili lakuti: Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino,+ choipa chimakhala chili ndi ine.+ 22 Mumtima mwanga+ ndimasangalala kwambiri+ ndi chilamulo cha Mulungu, 23 koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga+ chikumenyana+ ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga+ n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo+ chimene chili m’ziwalo zanga. 24 Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?+ 25 Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.+ Chotero, m’maganizo mwanga ineyo ndine kapolo wa chilamulo cha Mulungu,+ koma m’thupi langa ndine kapolo wa chilamulo cha uchimo.+
8 Chotero amene ali ogwirizana ndi Khristu Yesu alibe mlandu.+ 2 Pakuti chilamulo+ cha mzimu+ umene umapatsa moyo+ mwa Khristu Yesu chakumasulani+ ku chilamulo cha uchimo ndi cha imfa.+ 3 Mulungu anatsutsa uchimo mwa kugwiritsa ntchito thupi potumiza Mwana wake+ m’thupi lofanana ndi lauchimo+ kuti athane ndi uchimo.+ Pakuti Chilamulo sichinathe kuchita zimenezi+ pokhala chofooka+ chifukwa cha thupi. 4 Mulungu anachita izi kuti ife amene tikuyenda motsatira za mzimu,+ osati motsatira zofuna za thupi, tikwaniritse miyezo yolungama ya Chilamulo.+ 5 Chifukwa otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi,+ koma otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.+ 6 Pakuti kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa,+ koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu+ kumabweretsa moyo ndi mtendere, 7 chifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani+ ndi Mulungu, popeza thupi siligonjera+ chilamulo cha Mulungu, ndipotu kunena zoona, silingachigonjere. 8 Choncho, otsatira zofuna za thupi+ sangakondweretse Mulungu.
9 Komabe, inu mukutsatira za mzimu,+ osati za thupi, ngati mzimu wa Mulungu ukukhaladi mwa inu.+ Ngati wina alibe mzimu wa Khristu,+ ameneyu si wa Khristu. 10 Koma ngati Khristu ali wogwirizana ndi inu,+ ngakhale kuti thupi ndi lakufa chifukwa cha uchimo, mzimu ndiwo moyo+ chifukwa cha chilungamo. 11 Chotero, mzimu wa amene anaukitsa Yesu kwa akufa ukakhala mwa inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu kwa akufa+ adzachititsanso matupi anu otha kufawo kukhala ndi moyo+ mwa mzimu wake umene ukukhala mwa inu.
12 Choncho abale, tili ndi ngongole, osati kwa thupi kuti tizikhala motsatira zofuna za thupi.+ 13 Pakuti ngati mukukhala motsatira zofuna za thupi, ndiye kuti mosakayikira mudzafa.+ Koma mukapha zochita za thupi+ mwa mzimu, mudzakhala ndi moyo. 14 Onse amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewa ndiwo ana a Mulungu.+ 15 Popeza simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha,+ koma munalandira mzimu+ wakuti mukhale ana,+ umene timafuula nawo kuti: “Abba,*+ Atate!” 16 Pakuti mzimuwo+ umachitira umboni+ limodzi ndi mzimu wathu+ kuti ndife ana a Mulungu.+ 17 Chotero, ngati tili ana, tilinso olandira cholowa: Olandira cholowa a Mulungu, komanso olandira cholowa anzake+ a Khristu, malinga ngati tivutika+ naye limodzi kuti tikalandire ulemerero limodzi ndi iye.+
18 Ndiye chifukwa chake ndikuona kuti masautso+ amene tili nawo tsopano si kanthu powayerekeza ndi ulemerero+ umene udzaonekere kudzera mwa ife. 19 Pakuti chilengedwe+ chikudikira mwachidwi+ nthawi imene ulemelero wa ana a Mulungu udzaonekere.+ 20 Popeza chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake,+ osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa iye amene anachipereka, pa maziko a chiyembekezo+ 21 chakuti chilengedwecho+ chidzamasulidwa+ ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu. 22 Pakuti tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano. 23 Si zokhazo ayi, komanso ifeyo amene tili ndi zipatso zoyambirira+ zomwe ndi mzimu, tikubuula+ mumtima mwathu pamene tikudikira ndi mtima wonse kuti titengedwe kukhala ana a Mulungu,+ kumasulidwa ndi dipo* kuti tituluke m’matupi athu. 24 Pakuti tinapulumutsidwa tili ndi chiyembekezo chimenechi,+ koma chimene chikuyembekezedwa chikaoneka sichikhalanso choyembekezedwa, chifukwa munthu akaona chinthu chimene anali kuchiyembekezera, kodi amachiyembekezanso? 25 Koma ngati tikuyembekezera+ chimene sitikuchiona,+ timachidikirabe mopirira.+
26 Mofanana ndi zimenezi, mzimu+ umatithandiza pa zofooka zathu.+ Pakuti chimene tiyenera kupempherera monga mmene tiyenera kupemphera sitikuchidziwa,+ koma mzimu+ umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. 27 Koma iye amene amasanthula mitima+ amadziwa zimene mzimu ukutanthauza,+ chifukwa umachonderera m’malo mwa oyera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.+
28 Tikudziwa tsopano kuti Mulungu amagwirizanitsa zochita zake zonse+ pofuna kupindulitsa amene amakonda Mulungu, anthu oitanidwa mogwirizana ndi cholinga chake.+ 29 Amatero chifukwa amene anawadziwa choyamba+ anawasankhiratu+ kuti adzakhale ofanana+ ndi Mwana wake,+ kuti iye akhale woyamba kubadwa+ pakati pa abale ake ambiri.+ 30 Ndiponso, amene anawasankhiratu+ ndi amenenso anawaitana,+ ndipo amene anawaitanawo ndi amenenso anawayesa olungama.+ Kenako amene anawayesa olungama ndi amenenso anawapatsa ulemerero.+
31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+ 32 Iye amene sanaumire ngakhale Mwana wake+ koma anamupereka m’malo mwa ife tonse,+ angalephere bwanji kutipatsanso mokoma mtima zinthu zina zonse pamodzi ndi Mwana wakeyo?+ 33 Ndani adzasumira mlandu anthu a Mulungu ochita kusankhidwa?+ Mulungu ndiye amawayesa olungama.+ 34 Ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene anafa, zoonadi, amenetu anaukitsidwa kwa akufa. Iye ali kudzanja lamanja+ la Mulungu, ndipo amatilankhulira mochonderera kwa Mulunguyo.+
35 Ndani adzatilekanitsa ndi chikondi cha Khristu?+ Chisautso kodi, kapena zowawa, chizunzo, njala, usiwa, zoopsa, kapena lupanga?+ 36 Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse. Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.”+ 37 Koma tikugonjetsa zinthu zonsezi+ kudzera mwa iye amene anatikonda. 38 Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo,+ angelo,+ maboma,+ zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu,+ 39 msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+
9 Ndikunena zoona+ mwa Khristu, sindikunama ayi.+ Ine pamodzi ndi chikumbumtima changa tikuchitira umboni mwa mzimu woyera, 2 kuti ndili ndi chisoni chachikulu ndiponso mtima ukundipweteka nthawi zonse.+ 3 Ndikanakonda kuti ineyo ndichotsedwe kwa Khristu monga wotembereredwa m’malo mwa abale anga,+ amene ali anthu a mtundu wanga.+ 4 Amenewa ndi Aisiraeli,+ amene Mulungu anawatenga kukhala ana ake.+ Anawapatsanso ulemerero,+ mapangano,+ Chilamulo,+ utumiki wopatulika+ ndi malonjezo.+ 5 Iwo ndi ana a makolo akale aja.+ Komanso Khristu monga munthu,+ anatuluka pakati pawo. Mulungu,+ amene ndiye wamkulu pa zinthu zonse, atamandike kwamuyaya. Ame.
6 Komabe, sizili ngati kuti mawu a Mulungu analephera.+ Pakuti si onse ochokera kwa Isiraeli amene alidi “Aisiraeli.”+ 7 Ndiponso si onse amene ali ana chifukwa chongokhala mbewu ya Abulahamu.+ Koma Malemba amati, “Amene adzatchedwa ‘mbewu yako’ adzachokera mwa Isaki.”+ 8 Izi zikutanthauza kuti, si ana akuthupi+ amene alidi ana a Mulungu,+ koma ana a lonjezo+ ndiwo amayesedwa mbewu. 9 Popeza lonjezo lija linati: “Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ 10 Lonjezolo silinaperekedwe pa nthawi imeneyo yokha ayi, koma linaperekedwanso kwa Rabeka pamene anali ndi pakati pa mapasa+ a Isaki kholo lathu lija. 11 Mapasawo asanabadwe ndiponso asanachite chilichonse chabwino kapena choipa,+ kuti cholinga cha Mulungu powasankha chikhalebe chodalira Iye amene amaitana,+ osati chodalira ntchito, 12 Rabeka anauzidwa kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.”+ 13 Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Ndinakonda Yakobo, koma Esau ndinadana naye.”+
14 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Mulungu alibe chilungamo?+ Ayi si zimenezo! 15 Pakuti iye anauza Mose kuti: “Amene ndikufuna kumusonyeza chifundo, ndidzamusonyeza chifundo, ndipo ndidzamvera chisoni aliyense amene ndikufuna kumumvera chisoni.”+ 16 Chotero, sizidalira munthu wofunayo kapena amene akuthamanga, koma Mulungu,+ amene ali ndi chifundo.+ 17 Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+ 18 Chotero, iye amachitira chifundo munthu amene wafuna kumuchitira chifundo,+ koma amalola anthu ena kuti aumitse mitima yawo.+
19 Mwina unganene kwa ine kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani angatsutse chifuniro chake chimene chinanenedwa?”+ 20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+ 21 Kodi simudziwa kuti woumba mbiya+ ali ndi ufulu woumba chiwiya china cholemekezeka, china chonyozeka kuchokera pa dongo limodzi?+ 22 Bwanji ngati Mulungu analekerera moleza mtima kwambiri ziwiya za mkwiyo zoyenera kuwonongedwa ngakhale kuti akufuna kuonetsa mkwiyo wake ndi mphamvu zake?+ 23 Ndiponso bwanji ngati anachita zimenezo kuti asonyeze kukula kwa ulemerero wake+ kwa ziwiya+ zachifundo, zomwe anazikonzeratu kuti zikhale zaulemerero,+ 24 zimene ndi ifeyo amene anatiitana osati kuchokera mwa Ayuda okha komanso mwa mitundu ina?+ 25 Zilinso monga mmene ananenera m’buku la Hoseya kuti: “Anthu amene si anthu anga+ ndidzawatcha ‘anthu anga,’ ndipo mkazi amene sanali wokondedwa ndidzamutcha ‘wokondedwa.’+ 26 Ndipo pamalo pamene anauzidwapo kuti, ‘Inu sindinu anthu anga,’ pamalo omwewo adzatchedwa ‘ana a Mulungu wamoyo.’”+
27 Komanso, Yesaya analankhula mofuula zokhudza Isiraeli kuti: “Ngakhale kuti ana a Isiraeli adzakhala ochuluka ngati mchenga wa m’nyanja,+ ndi ochepa okha amene adzapulumuke.+ 28 Pakuti Yehova adzazenga milandu padziko lapansi, ndi kuimaliza yonse mwachangu.”+ 29 Ndiponso, monga Yesaya ananeneratu kuti: “Yehova wa makamu+ akanapanda kutisiyira mbewu, tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.”+
30 Ndiye tinene kuti chiyani? Tinene kuti, ngakhale kuti anthu a mitundu ina sanatsatire chilungamo, iwo anapeza chilungamo+ chimene chimapezeka chifukwa cha chikhulupiriro.+ 31 Koma ngakhale kuti Aisiraeli anali kutsatira lamulo la chilungamo, sanalipeze lamulolo.+ 32 Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iwo sanalitsatire mwa chikhulupiriro, koma malinga ndi kuganiza kwawo, analitsatira mwa ntchito.+ Iwo anakhumudwa “pamwala wokhumudwitsa”+ 33 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Inetu ndikuika mwala+ wopunthwitsa ndiponso mwala wokhumudwitsa+ m’Ziyoni, koma munthu wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”+
10 Ndithu abale, chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzero langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe.+ 2 Pakuti ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka+ potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.+ 3 Ndipo posadziwa chilungamo cha Mulungu,+ iwo sanagonjere chilungamocho+ koma anayesetsa kukhazikitsa chawochawo.+ 4 Pakuti Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo,+ kuti aliyense wokhulupirira akhale wolungama.+
5 Pajatu Mose analemba kuti munthu wochita chilungamo cha m’Chilamulo adzakhala ndi moyo chifukwa cha chilungamo chimenecho.+ 6 Koma za chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro, Malemba amati: “Mumtima mwako usanene kuti,+ ‘Kodi ndani adzakwera kumwamba?’+ kuti akatsitse Khristu.+ 7 Kapena, ‘Kodi ndani adzatsikira kuphompho?’+ kuti akaukitse Khristu kwa akufa.”+ 8 Koma kodi Lemba limati chiyani? Limati: “Mawu a chilamulowo ali pafupi ndi iwe, ali m’kamwa mwako ndi mumtima mwako,”+ amenewa ndi “mawu”+ a chikhulupiriro, amene tikulalikira.+ 9 Pakuti ngati ukulengeza kwa anthu ‘mawu amene ali m’kamwa mwakowo,’+ akuti Yesu ndiye Ambuye,+ ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa,+ udzapulumuka.+ 10 Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake+ kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera+ chikhulupiriro chake kuti apulumuke.
11 Paja Lemba limati: “Palibe wokhulupirira iye,+ amene adzakhumudwe.”+ 12 Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki,+ popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi, amene amapereka mowolowa manja+ kwa onse oitana pa dzina lake. 13 Pakuti “aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”+ 14 Komabe, kodi angaitane bwanji munthu amene samukhulupirira?+ Angakhulupirire bwanji munthu amene sanamvepo za iye? Angamve bwanji za iye popanda wina kulalikira?+ 15 Ndipo angalalikire bwanji ngati sanatumidwe?+ Zili monga muja Malemba amanenera kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwabasi!”+
16 Ngakhale zili choncho, si onse amene analabadira uthenga wabwino.+ Pakuti Yesaya anati: “Yehova, kodi ndani wakhulupirira zimene anamva kwa ife?”+ 17 Chotero munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.+ Ndipo zimene wamvazo zimachokera m’mawu onena za Khristu.+ 18 Koma ndifunsebe kuti, Kodi kumva sanamve? Pajatu “liwu lawo linamveka padziko lonse lapansi,+ ndipo mawu awo anamveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”+ 19 Komabe ndifunse kuti, Kodi si zoona kuti Aisiraeli anadziwa?+ Choyamba Mose anati: “Ndidzakuchititsani nsanje kudzera mwa anthu omwe si mtundu. Ndidzaputa mkwiyo wanu woopsa kudzera mwa mtundu wopusa.”+ 20 Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambiri kuti: “Anthu amene anandipeza ndi amene sanali kundifunafuna.+ Ndinaonekera kwa anthu amene sanafunse za ine kuti andipeze.”+ 21 Koma za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamva+ komanso otsutsa.”+
11 Ndiye ndifunse kuti, kodi Mulungu anakana anthu ake?+ Ayi ndithu! Paja inenso ndine Mwisiraeli,+ wa mbewu ya Abulahamu, wa fuko la Benjamini.+ 2 Mulungu sanakane anthu ake amene anali oyambirira kuwavomereza.+ Kodi ndithu simukudziwa kuti Lemba limati chiyani za Eliya, pamene anali kuchonderera Mulungu motsutsa Aisiraeli?+ Limati: 3 “Yehova, iwo apha aneneri anu, agumula maguwa anu ansembe, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano akufunafuna moyo wanga.”+ 4 Koma kodi mawu a Mulungu+ anati chiyani kwa iyeyo? Anati: “Ndadzisungira anthu 7,000, amene sanagwadire Baala.”+ 5 Chotero, pa nthawi ino alipo ena ochepa+ amene anasankhidwa+ mwa kukoma mtima kwakukulu. 6 Ndiyetu ngati anasankhidwa mwa kukoma mtima kwakukulu,+ sanasankhidwe chifukwa cha ntchito zawo ayi.+ Zitati zitero, kukoma mtima kumeneko sikungakhalenso kukoma mtima kwakukulu.+
7 Ndiye zili bwanji pamenepa? Chimene Aisiraeli akuchifunitsitsa sanachipeze,+ koma anthu osankhidwa+ ndi amene anachipeza. Enawo anaumitsa mitima yawo+ 8 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tatikulu,+ maso osaona ndi makutu osatha kumva, kufikira lero.”+ 9 Ndiponso Davide anati: “Tebulo lawo likhale msampha, mbuna, chopunthwitsa ndi chilango kwa iwo.+ 10 Maso awo achite mdima kuti asaone, ndipo weramitsani msana wawo nthawi zonse.”+
11 Ndiyeno ndifunse, Kodi anapunthwa mpaka kugweratu?+ Ayi! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo+ pali chipulumutso kwa anthu a mitundu ina,+ kuti olakwawo achite nsanje.+ 12 Chotero ngati kulakwa kwawo kukutanthauza chuma ku dziko, ndipo kuchepa kwawo kukutanthauza chuma kwa anthu a mitundu ina,+ bwanji nanga za chiwerengero chawo chokwanira?+ Chidzatanthauzatu zazikulu kuposa pamenepo!
13 Tsopano ndikulankhula kwa inu ochokera m’mitundu ina. Malinga n’kuti ndine mtumwi+ weniweni wotumidwa kwa mitundu ina,+ ndimalemekeza+ utumiki wanga,+ 14 kuti mwina ndingapangitse anthu a mtundu wanga kuchita nsanje ndi kupulumutsapo+ ena a iwo.+ 15 Chifukwa ngati dziko layanjidwa ndi Mulungu chifukwa chakuti iwo anatayidwa,+ ndiye kuti akadzalandiridwa+ zidzatanthauza moyo kuchokera ku imfa. 16 Ndiponso, ngati mbali ya mtanda imene yadyedwa monga chipatso choyambirira+ ili yoyera, ndiye kuti mtanda wonse ndi woyeranso. Ngati muzu uli woyera,+ ndiye kuti nthambi nazonso ndi zoyera.
17 Ngati nthambi zina zinadulidwa, koma iwe ngakhale kuti ndiwe nthambi ya mtengo wa maolivi wam’tchire, unalumikizidwa pakati pa nthambi zotsala+ ndipo unayamba kugawana nawo muzu wamafuta+ wa mtengo wa maoliviwo,+ 18 usakondwere monyoza nthambi zimene zinadulidwazo. Koma ngati ukunyoza nthambizo,+ kumbukira kuti si iwe amene ukuchirikiza muzu,+ koma muzu ndi umene ukuchirikiza iweyo.+ 19 Komatu tsopano unganene kuti: “Nthambi zina zinadulidwa+ kuti alumikizepo ine.”+ 20 N’zoonadi! Iwo anadulidwa chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo waimirira chifukwa cha chikhulupiriro.+ Taya maganizo odzikuzawo,+ koma khala ndi mantha.+ 21 Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachilengedwe, sadzakulekereranso iweyo.+ 22 Choncho taona kukoma mtima+ komanso kusalekerera+ kwa Mulungu. Amene anagwa anaona kusalekerera+ kwake, koma iweyo ukuona kukoma mtima kwa Mulungu, malinga ngati ukukhalabe+ m’kukoma mtima kwake. Apo ayi, iwenso udzadulidwa.+ 23 Iwonso ngati angayambe kukhala ndi chikhulupiriro, adzalumikizidwa kumtengowo,+ pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24 Ngati iweyo unadulidwa kumtengo wa maolivi umene mwachilengedwe umamera m’tchire, ndipo mosemphana ndi chilengedwe, unalumikizidwa+ kumtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si kwapafupi kulumikiza nthambi izi kumtengo wawo umene zinadulidwako?+
25 Pakuti sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale za chinsinsi chopatulika+ chimenechi, kuopera kuti mungadzione ngati ochenjera. Chinsinsi chopatulikacho n’chakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo+ mpaka chiwerengero chonse+ cha anthu ochokera m’mitundu ina chitakwanira.+ 26 Mwa njira imeneyi, Aisiraeli onse+ adzapulumuka. Izi zikugwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Wolanditsa adzachokera m’Ziyoni+ ndi kuchotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu.+ 27 Limeneli lidzakhala pangano langa ndi iwo,+ pamene ndidzawachotsera machimo awo.”+ 28 Zoonadi, pa nkhani ya uthenga wabwino iwo ndi adani a Mulungu, ndipo zimenezi zapindulitsa inu.+ Koma kunena za kusankha kwa Mulungu, iwo ndi okondedwa ake chifukwa cha makolo awo oyambirira.+ 29 Mulungu sadzadandaula+ chifukwa cha mphatso zake ndiponso chifukwa chakuti anawaitana. 30 Pakuti monga mmene inuyo munalili osamvera+ Mulungu koma tsopano mwasonyezedwa chifundo+ chifukwa cha kusamvera kwawo,+ 31 iwowa tsopano akhala osamvera, zimene zapangitsa kuti inuyo musonyezedwe chifundo,+ kuti iwonso tsopano asonyezedwe chifundo. 32 Popeza Mulungu walola onse kuti akhale akaidi a kusamvera,+ kuti onsewo awasonyeze chifundo.+
33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake? 34 Pakuti “ndani akudziwa maganizo a Yehova,+ kapena ndani angakhale phungu wake?”+ 35 Kapenanso, “Ndani anayamba kumupatsa kanthu, kuti amubwezere?”+ 36 Chifukwa zinthu zonse zimachokera kwa iye ndipo iye ndi amene anazipanga ndiponso ndi zake.+ Ulemerero ukhale wake kwamuyaya.+ Ame.
12 Chotero ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu abale, kuti mupereke matupi anu+ ngati nsembe+ yamoyo,+ yoyera+ ndi yovomerezeka kwa Mulungu,+ ndiyo utumiki wopatulika+ mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.+ 2 Musamatengere+ nzeru za nthawi* ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu,+ kuti muzindikire+ chimene chili chifuniro+ cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.
3 Pakuti mwa kukoma mtima kwakukulu kumene ndinapatsidwa, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.+ Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino,+ malinga ndi chikhulupiriro+ chimene Mulungu wamupatsa.+ 4 Pakuti monga tilili ndi ziwalo zambiri+ m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana, 5 momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambiri, tili thupi limodzi+ mwa Khristu, ndipo aliyense payekha ndi chiwalo cha mnzake.+ 6 Chotero, popeza kuti tili ndi mphatso zosiyanasiyana+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu+ kumene tinapatsidwa, kaya tili ndi mphatso ya ulosi, tiyeni tilosere malinga ndi chikhulupiriro chimene tapatsidwa. 7 Ngati tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni tichitebe utumikiwo.+ Amene akuphunzitsa,+ aziphunzitsa ndithu.+ 8 Wochenjeza, aike mtima wake pa kuchenjeza.+ Wogawa, agawe mowolowa manja.+ Wotsogolera,+ atsogolere mwakhama. Ndipo wosonyeza chifundo,+ achite zimenezo mokondwa.
9 Chikondi+ chanu chisakhale cha chiphamaso.+ Nyansidwani ndi choipa,+ gwiritsitsani chabwino.+ 10 Pokonda abale,+ khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu,+ khalani patsogolo. 11 Musakhale aulesi pa ntchito yanu.+ Yakani ndi mzimu.+ Tumikirani Yehova monga akapolo.+ 12 Kondwerani ndi chiyembekezocho.+ Pirirani chisautso.+ Limbikirani kupemphera.+ 13 Gawanani ndi oyera malinga ndi zosowa zawo.+ Khalani ochereza.+ 14 Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani.+ Muzidalitsa,+ osatemberera ayi.+ 15 Sangalalani ndi anthu amene akusangalala.+ Lirani ndi anthu amene akulira. 16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera.+ Musamaganize modzikweza,+ koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musadziyese anzeru.+
17 Musabwezere choipa pa choipa.+ Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino. 18 Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere+ ndi anthu onse, monga mmene mungathere. 19 Okondedwa, musabwezere choipa,+ koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Pakuti Malemba amati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.”+ 20 Koma “ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa.+ Pakuti mwa kutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.”+ 21 Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.+
13 Munthu aliyense azimvera+ olamulira akuluakulu,+ chifukwa palibe ulamuliro+ umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola.+ Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana+ mololedwa ndi Mulungu.+ 2 Chotero amene akutsutsana ndi ulamuliro akutsutsana ndi dongosolo la Mulungu. Amene akutsutsana ndi dongosolo limeneli adzalandira chiweruzo.+ 3 Pakuti olamulira amaopsa ngati ukuchita zoipa,+ osati ngati ukuchita zabwino. Choncho kodi ukufuna kuti usamachite mantha ndi olamulira? Pitiriza kuchita zabwino,+ ndipo olamulira adzakutamanda. 4 Olamulirawo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zikuyendere bwino.+ Koma ngati ukuchita zoipa,+ chita mantha chifukwa sagwira lupanga pachabe, pakuti iye ndi mtumiki wa Mulungu wosonyeza mkwiyo wa Mulungu kwa munthu wochita zoipa.+
5 Chotero pali chifukwa chabwino chakuti anthu inu mukhalire ogonjera, osati chabe chifukwa choopa mkwiyo umenewo, komanso chifukwa cha chikumbumtima chanu.+ 6 N’chifukwa chake mumakhomanso misonkho, pakuti iwo ndi antchito a Mulungu otumikira anthu,+ ndipo akukwaniritsa cholinga chimenechi nthawi zonse. 7 Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho.+ Amene amafuna ndalama ya chiphaso, m’patseni ndalama ya chiphaso. Amene amafuna kuopedwa, muopeni.+ Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.+
8 Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense,+ kusiyapo kukondana,+ popeza amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa chilamulo.+ 9 Chifukwa malamulo onena kuti, “Usachite chigololo,+ Usaphe munthu,+ Usabe,+ Usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili m’mawu awa akuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 10 Chikondi+ sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake,+ chotero chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.+
11 Chitani zimenezi, makamakanso chifukwa chakuti nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu ola lakuti mudzuke ku tulo,+ pakuti chipulumutso chathu chili pafupi kwambiri tsopano kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupirira.+ 12 Usiku uli pafupi kutha, usana wayandikira.+ Chotero tiyeni tivule ntchito za mdima+ ndipo tivale zida za kuwala.+ 13 Tiyeni tiyende moyenera+ monga usana, osati m’maphwando aphokoso ndi kumwa mwauchidakwa,*+ osati m’chiwerewere ndi khalidwe lotayirira,+ ndiponso osati m’mikangano+ ndi nsanje. 14 Koma valani Ambuye Yesu Khristu,+ ndipo musamakonzekere kuchita zilakolako za thupi.+
14 Landirani munthu wokhala ndi zofooka m’chikhulupiriro+ chake, koma osagamula pa zoganiza za mumtima mwake.+ 2 Wina ali ndi chikhulupiriro chakuti angadye china chilichonse,+ koma munthu wofooka amadya zamasamba. 3 Amene amadya, asanyoze amene sadya,+ ndipo wosadyayo asaweruze amene amadya, popeza ameneyo analandiridwa ndi Mulungu. 4 Ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wapakhomo wa mnzako?+ Ndi udindo wa bwana wake kumuweruza kuti ndi wolakwa kapena wosalakwa.+ Komatu Yehova akhoza kumukomera mtima chifukwa angathe kumuthandiza.+
5 Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake,+ koma wina amaona tsiku lina mofanana ndi masiku ena onse.+ Choncho munthu aliyense akhale wotsimikiza ndi mtima wonse m’maganizo mwake. 6 Amene amasunga tsiku amalisungira kulemekeza Yehova. Amene amadya, amadya kuti alemekeze Yehova,+ chifukwa amayamika Mulungu.+ Amene sadya, sadya pofuna kulemekeza Yehova,+ chifukwa nayenso amayamika Mulungu.+ 7 Kunena zoona, palibe aliyense wa ife amene amakhala ndi moyo kuti adzilemekeze yekha,+ ndipo palibe amene amafa kuti adzilemekeze yekha. 8 Pakuti tikakhala ndi moyo, timakhalira moyo Yehova,*+ ndipo tikafa, timafera Yehova.+ Chotero kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.+ 9 Ndiye chifukwa chake Khristu anafa n’kukhalanso ndi moyo,+ kuti akhale Ambuye wa akufa+ ndiponso wa amoyo.+
10 Nanga n’chifukwa chiyani umaweruza m’bale wako?+ Kapenanso n’chifukwa chiyani umanyoza m’bale wako? Pakuti tonse tidzaimirira patsogolo pa mpando woweruzira milandu+ wa Mulungu. 11 Malembatu amati: “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova,+ ‘bondo lililonse lidzandigwadira ine, ndipo lilime lililonse lidzavomereza poyera kwa Mulungu.’”+ 12 Chotero aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.+
13 Pa chifukwa chimenechi, tisamaweruzane,+ koma m’malomwake tsimikizani mtima+ kuti simuikira m’bale wanu+ chokhumudwitsa+ kapena chopunthwitsa. 14 Ndikudziwa ndipo ndikukhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti palibe chakudya chodetsedwa mwa icho chokha.+ Koma ngati munthu akuona chinachake monga chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa.+ 15 Chifukwa ngati m’bale wako akuvutika maganizo chifukwa cha chakudya, ndiye kuti simukuyendanso m’chikondi.+ Musawononge* munthu amene Khristu anamufera+ chifukwa cha zakudya zanu. 16 Choncho musalole kuti anthu akunenereni zoipa pa zabwino zimene mukuchita. 17 Pakuti ufumu wa Mulungu+ si kudya ndi kumwa ayi,+ koma chilungamo,+ mtendere+ ndi chimwemwe+ zobwera ndi mzimu woyera. 18 Chifukwa aliyense wotumikira Khristu motere ali wovomerezeka kwa Mulungu ndipo anthu amakondwera naye.+
19 Choncho, tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere+ ndiponso zolimbikitsana.+ 20 Siyani kuwononga ntchito ya Mulungu chifukwa cha zakudya basi.+ Zoonadi, zinthu zonse ndi zoyera, koma munthu amene amadya ngakhale pamene akukhumudwitsa ena, amalakwa.+ 21 Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.+ 22 Chikhulupiriro chimene uli nacho, khala nacho pakati pa iweyo ndi Mulungu.+ Wodala munthu amene sakudziika pa chiweruzo ndi zinthu zimene wasankha kuchita. 23 Koma ngati akudya ndipo akukayikira, ameneyo watsutsidwa kale,+ chifukwa sakudya mwa chikhulupiriro. Ndithu, chilichonse chochitidwa mosemphana ndi chikhulupiriro ndi tchimo.+
15 Ife olimba tiyenera kunyamula zofooka za osalimba,+ osati kumadzikondweretsa tokha ayi.+ 2 Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa.+ 3 Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha,+ koma anachita mmene Malemba amanenera kuti: “Mnyozo wa anthu amene anali kukutonzani wagwa pa ine.”+ 4 Zinthu zonse zimene zinalembedwa+ kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.+ Malembawa amatipatsa chiyembekezo+ chifukwa amatithandiza kupirira+ ndiponso amatilimbikitsa.+ 5 Tsopano, Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza, achititse nonsenu kukhala ndi maganizo+ amene Khristu Yesu anali nawo, 6 kuti nonse pamodzi,+ ndi pakamwa pamodzi, mulemekeze Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
7 Chotero landiranani,+ monga mmene Khristu anatilandirira,+ kuti ulemerero upite kwa Mulungu. 8 Kunena zoona,+ Khristu anakhaladi mtumiki+ kwa anthu odulidwa+ kuti atsimikizire kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Komanso iye anasonyeza kuti malonjezo+ amene Mulunguyo anapatsa makolo awo ndi otsimikizirika, 9 kuti mitundu ina+ ipereke ulemerero kwa Mulungu chifukwa cha chifundo+ chake, monga mmene Malemba amanenera kuti: “N’chifukwa chake ndidzakuvomerezani poyera pakati pa mitundu. Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ 10 Komanso Malemba amati: “Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.”+ 11 Ndiponso amati: “Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu, ndipo anthu onse amutamande.”+ 12 Komanso Yesaya anati: “Padzakhala muzu wa Jese,+ ndipo padzatuluka wina wodzalamulira mitundu.+ Mitundu idzayembekezera iye.”+ 13 Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwanu, kuti mukhale ndi chiyembekezo chachikulu mwa mphamvu ya mzimu woyera.+
14 Tsopano abale anga, ine ndine wotsimikiza mtima za inu kuti ndinu okonzeka kuchita zabwino, monga mmene mwakhalira odziwa zinthu zonse.+ Ndine wotsimikizanso mtima kuti mukhoza kulangizana.+ 15 Komabe, ndakulemberani mfundo zina mosapita m’mbali kuti ndikukumbutseninso.+ Ndachita zimenezi chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wandipatsa.+ 16 Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku kuti ndigwire ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu monga wantchito wa Khristu Yesu, wotumikira anthu a mitundu ina.+ Cholinga changa pogwira ntchito yopatulikayi+ n’chakuti mitundu ina ya anthu iperekedwe+ kwa Mulungu ngati mphatso yovomerezeka+ imene yayeretsedwa ndi mzimu woyera.+
17 Chotero ndili ndi chifukwa chokhalira wokondwa mwa Khristu Yesu+ pa zinthu zokhudza Mulungu.+ 18 Pakuti sindidzayesa m’pang’ono pomwe kulankhula kanthu ngakhale kamodzi kokha ngati sikanachokere m’zinthu zimene Khristu anachita mwa ine+ kuti mitundu ina ikhale yomvera.+ Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mawu anga+ ndi zochita zanga, 19 ndiponso pogwiritsa ntchito mphamvu yochita zizindikiro ndi zinthu zodabwitsa zolosera zam’tsogolo,+ mwa mphamvu ya mzimu woyera. Chotero ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu+ kuyambira ku Yerusalemu, kuzungulira+ mpaka ku Iluriko. 20 Ndithudi, pochita zimenezi ndinatsimikiza mtima kuti ndisalengeze uthenga wabwino kumene Khristu anatchulidwa kale, ndi cholinga chakuti ndisamange pamaziko+ a munthu wina, 21 koma ndichite monga mmene Malemba amanenera kuti: “Amene chilengezo chonena za iye sichinawapeze adzaona, ndipo amene sanamve adzazindikira.”+
22 Choncho, pa chifukwa chimenechinso ndinalephera kufika kwa inu.+ 23 Koma tsopano popeza kulibenso gawo limene sindinafikeko m’madera amenewa, ndiponso popeza kuti kwa zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kufika kwanuko,+ 24 ndili ndi chikhulupiriro kuti mulimonse mmene zingakhalire, pa ulendo wanga wa ku Sipaniya+ nthawi ina iliyonse, ndidzaonana nanu. Ndikadzacheza nanu mpaka kukhutira, mudzandiperekeza+ pa ulendo wangawo. 25 Koma tsopano ndatsala pang’ono kupita ku Yerusalemu kukatumikira oyera.+ 26 Abale amene ali ku Makedoniya ndi ku Akaya+ akhala ali ofunitsitsa kupereka+ mphatso kwa oyera osauka a ku Yerusalemu. 27 Ndi zoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Pakuti ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu+ kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti anthu a mitundu inawo ayeneranso kutumikira oyera amenewa mwa kuwapatsa zinthu zofunika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.+ 28 Choncho ndikakamaliza zimenezi ndipo ndikakafika bwino ndi zopereka zimenezi+ kwa iwo, ndidzadzera kwanuko popita ku Sipaniya.+ 29 Komanso, ndikudziwa kuti ndikadzafika kwanuko ndidzafika ndi dalitso lonse lochokera kwa Khristu.+
30 Chotero ndikukudandaulirani abale, kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi mwa chikondi cha mzimu,+ kuti mulimbikire limodzi ndi ine popemphera kwa Mulungu za ineyo.+ 31 Tilimbikire kupemphera kuti ndikalanditsidwe+ kwa anthu osakhulupirira a ku Yudeya, ndi kutinso utumiki wanga wa ku Yerusalemu+ ukakhale wolandirika kwa oyerawo,+ 32 kuti ndikadzafika kwa inu ndi chisangalalo mwa kufuna kwa Mulungu, tidzalimbikitsidwe pamodzi.+ 33 Mulungu amene amapatsa mtendere akhale ndi nonsenu.+ Ame.
16 Ndikufuna kukudziwitsani za mlongo wathu Febe, amene akutumikira+ mumpingo wa ku Kenkereya.+ 2 Mulandireni+ mwa Ambuye mmene mumalandirira oyerawo, ndi kumuthandiza pa nkhani iliyonse imene angafune thandizo lanu.+ Pakuti iyenso anateteza abale ambirimbiri, ngakhalenso ineyo.
3 Mundiperekere moni kwa Purisika ndi Akula,+ antchito anzanga+ mwa Khristu Yesu. 4 Iwo anaika miyoyo+ yawo pachiswe chifukwa cha moyo wanga, ndipo si ine ndekha amene ndikuwayamikira,+ komanso mipingo yonse ya anthu a mitundu ina. 5 Ndikuperekanso moni ku mpingo umene umasonkhana m’nyumba mwawo.+ Moni kwa wokondedwa wanga Epeneto, amene ndi chipatso choyambirira+ cha Khristu mu Asia. 6 Moni kwa Mariya, amene wakuchitirani ntchito zambiri. 7 Moni kwa Anduroniko ndi Yuniya, omwe ndi achibale anga+ ndi akaidi anzanga.+ Amenewa ndi amuna odziwika kwambiri kwa atumwi ndiponso akhala ogwirizana+ ndi Khristu kwa nthawi yaitali kuposa ine.
8 Mundiperekere moni+ kwa Ampiliato, wokondedwa wanga mwa Ambuye. 9 Moni kwa Uribano wantchito mnzathu mwa Khristu, ndi wokondedwa wanga Sitaku. 10 Moni+ kwa Apele, wokhulupirika mwa Khristu. Moni kwa a m’banja la Arisitobulo. 11 Moni kwa wachibale wanga+ Herodiona. Moni kwa a m’banja la Narikiso amene ali mwa Ambuye.+ 12 Moni kwa Turufena ndi Turufosa, akazi ogwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye. Moni kwa Peresida, wokondedwa wathu. Mayi ameneyu wachita ntchito zambiri potumikira Ambuye. 13 Moni kwa Rufu, wochita kusankhidwa mwa Ambuye. Moninso kwa mayi ake amenenso ndi mayi anga. 14 Moni kwa Asunkirito, Felego, Heme, Pateroba, Heremase ndi abale amene ali nawo. 15 Moni kwa Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mlongo wake, komanso Olumpa, ndi oyera onse amene ali nawo.+ 16 Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwaubale.+ Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.
17 Tsopano ndikukudandaulirani abale, kuti musamale ndi anthu amene amayambitsa magawano+ ndi kuchita zinthu zokhumudwitsa ena. Zimenezi ndi zosemphana ndi chiphunzitso+ chimene munaphunzira, choncho muziwapewa.+ 18 Pakuti anthu oterowo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a mimba zawo.+ Ndipo mwa kulankhula mawu okopa+ ndi achinyengo+ amanyenga anthu oona mtima. 19 Pakuti anthu onse+ adziwa kuti ndinu omvera. Choncho ndikusangalala chifukwa cha inu. Koma ndikufuna kuti mukhale anzeru+ pa zinthu zabwino, ndi osadziwa+ kanthu pa zinthu zoipa.+ 20 Mulungu amene amapatsa mtendere+ aphwanya Satana+ pansi pa mapazi anu posachedwapa. Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu kukhale ndi inu.+
21 Wantchito mnzanga Timoteyo akupereka moni, chimodzimodzinso Lukiyo, Yasoni ndi Sosipato omwe ndi achibale anga.+
22 Ineyo Teritio, amene ndalemba kalatayi, ndikuti moni mwa Ambuye.
23 Gayo,+ amene akundichereza ndiponso mpingo wonse, akupereka moni. Erasito woyang’anira mzinda,+ ndi Kwarito m’bale wake akupereka moni. 24* ——
25 Tsopano Mulungu+ angakulimbitseni mwa uthenga wabwino umene ndikulengeza ndiponso mwa uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthenga wabwino umenewu ndi wogwirizana ndi zimene zaululidwa zokhudza chinsinsi chopatulika+ chimene chakhala chobisika kuyambira nthawi zakale. 26 Koma tsopano chinsinsi chopatulika chimenechi chaonetsedwa+ ndipo chadziwika pakati pa mitundu yonse ya anthu kudzera m’malemba aulosi. Zimenezi n’zogwirizana ndi lamulo la Mulungu wokhalako kwamuyaya. Cholinga chake n’chakuti anthu a mitundu yonse amukhulupirire ndi kumumvera mwa chikhulupiriro.+ 27 Kwa Mulungu wanzeru yekhayo,+ kukhale ulemerero+ kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu.+ Ame.
Mawu achiaramu otanthauza “ababa,” kapena, “Bambo anga!”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 2.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa n’cholinga chofuna kuledzera.
Onani Zakumapeto 2.
Kutanthauza kuwononga chikhulupiriro kapena chiyembekezo cha moyo wosatha wa m’tsogolo.
Pavesili m’mipukutu ina yachigiriki pali mawu akuti, “Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale ndi inu nonse. Ame.” Mawu amenewa akufanana ndi amene ali mu vesi 20. Koma mawuwa sapezeka m’mipukutu yakale kwambiri yachigiriki.