Kalata Yachiwiri kwa Akorinto
1 Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu, ndikulembera mpingo wa Mulungu wa ku Korinto, pamodzi ndi oyera onse+ amene ali mu Akaya+ monse, ndili limodzi ndi Timoteyo+ m’bale wathu, kuti:
2 Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+
3 Atamandike Mulungu ndi Atate+ wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wachifundo chachikulu+ ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,+ 4 amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse,+ kuti tithe kutonthoza+ amene ali m’masautso amtundu uliwonse, chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.+ 5 Popeza tikukumana ndi masautso ambiri chifukwa cha Khristu,+ tikutonthozedwanso kwambiri kudzera mwa Khristu.+ 6 Tsopano ngati tili m’masautso, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa.+ Ngati tikutonthozedwa, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe kuti mupirire masautso amene ifenso tikukumana nawo.+ 7 Chotero chiyembekezo chathu mwa inu sichikugwedera, podziwa kuti mukukumana ndi masautso ofanana ndi amene ifeyo tikukumana nawo, inunso mudzatonthozedwa ngati ifeyo.+
8 Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo m’chigawo cha Asia,+ pamene tinali pa vuto lalikulu lotiposa mphamvu, moti tinalibenso chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.+ 9 Ngakhalenso m’mitima mwathu, tinali kumva ngati talandira chiweruzo cha imfa. Zinatero kuti tisakhale ndi chikhulupiriro mwa ife tokha,+ koma mwa Mulungu amene amaukitsa akufa.+ 10 Iye anatipulumutsadi ku chinthu choopsa, ndicho imfa, ndipo adzatipulumutsabe.+ Tikukhulupirira kuti iye apitiriza kutipulumutsa.+ 11 Inunso mungathandizepo mwa kutiperekera mapembedzero anu,+ kuti pakhale anthu ambiri otiperekera mapemphero oyamikira+ zinthu zimene tapatsidwa mokoma mtima, chifukwa cha mapemphero a anthu ambiri.+
12 Ifeyo tili ndi chifukwa chodzitamandira chakuti m’dzikoli, makamaka pakati pa inuyo, tachita zinthu zoyera ndiponso moona mtima mogwirizana ndi zimene Mulungu amaphunzitsa. Tachita zimenezi osati modalira nzeru+ za m’dzikoli koma modalira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndipo chikumbumtima chathu chikuchitiranso umboni zimenezi.+ 13 Pakuti zimene takulemberanizi si zina ayi, koma zimene mukuzidziwa bwino ndiponso zimene mukuzivomereza. Ndili ndi chikhulupiriro choti mupitiriza kuvomereza zinthu zimenezi mpaka pa mapeto.+ 14 Inuyo mwavomereza kale, ngakhale kuti m’pang’ono pokha, kuti ifeyo ndife chifukwa choti mudzitamandire,+ ngati mmene inuyonso mudzakhalire chifukwa choti ifeyo tidzadzitamandire m’tsiku la Ambuye wathu Yesu.+
15 Choncho, popeza ndine wotsimikiza za zimenezi, ndinali ndi cholinga chofika kwa inu poyamba,+ kuti mudzakhale ndi mwayi wachiwiri+ wosangalala. 16 Kuti ndikadzacheza nanu pang’ono ndidzapite ku Makedoniya,+ ndipo ndikadzachoka ku Makedoniya ndidzabwerenso kwa inu+ kuti mudzandiperekeze+ popita ku Yudeya. 17 Tsopano pamene ndinali ndi cholinga chimenechi, kodi ndinali kulingalira mwachibwana?+ Kapena kodi zimene ndimaganiza kuti ndichite, ndimaziganiza ndi zolinga zadyera,+ kuti ndikati “Inde, inde” nthawi yomweyo ndisinthe ndinene kuti “Ayi, ayi”?+ 18 Koma Mulungu ndi wodalirika kuti mawu athu kwa inu asakhale Inde kenako Ayi. 19 Pakuti Mwana wa Mulungu,+ Khristu Yesu, amene analalikidwa pakati panu kudzera mwa ineyo, Silivano, ndi Timoteyo,+ sanakhale Inde kenako Ayi, koma mwa iye, Inde wakhalabe Inde.+ 20 Ndiponso malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani,+ akhala Inde kudzera mwa iye.+ Choteronso kudzera mwa iye, “Ame”+ amanenedwa kwa Mulungu kuti Mulungu alandire ulemerero kudzera mwa ife. 21 Koma amene amatitsimikizira kuti inuyo ndi ife tili a Khristu, amenenso anatidzoza,+ ndiye Mulungu. 22 Iye watiikanso chidindo+ chake chotitsimikizira ndipo watipatsa m’mitima mwathu chikole+ cha madalitso am’tsogolo, ndicho mzimu.+
23 Mulungu akhale mboni+ pa moyo wanga kuti chifukwa chimene sindinabwererebe ku Korintoko n’chakuti sindinafune kuti ndidzawonjezere chisoni chanu.+ 24 Sikuti ndife olamulira+ chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu+ kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika+ chifukwa cha chikhulupiriro chanu.+
2 Ndasankha mumtima mwanga kuti pobweranso kwa inu ndisadzakhalenso wachisoni.+ 2 Pakuti ngati ndingakuchititseni kumva chisoni,+ adzandisangalatsa ndani kupatulapo amene ndawachititsa kumva chisoniwo? 3 N’chifukwa chake ndinalemba zimenezi, kuti ndikadzabwera kumeneko, ndisadzakhale wachisoni+ chifukwa cha anthu amene ndiyenera kusangalala nawo.+ Pakuti ndili ndi chikhulupiriro+ mwa nonsenu kuti chimwemwe chimene ndili nacho ndi chimenenso nonsenu muli nacho. 4 Inetu ndinakulemberani kalata ija ndikusautsika ndi kuzunzika kwambiri mumtima, pamodzi ndi misozi yambiri,+ osati kuti muchite chisoni,+ koma kuti mudziwe chikondi chimene ndili nacho makamaka pa inu.
5 Ngati wina wachita kanthu kochititsa chisoni,+ sanachititse chisoni ineyo, koma mwanjira ina wachititsa chisoni nonsenu. Komabe sindikufuna kutsindika mfundo imeneyi mwamphamvu kwambiri. 6 Kudzudzulidwa+ ndi anthu ambiri chonchi n’kokwanira kwa munthu ameneyu. 7 Chotero tsopano mukhululukireni ndi mtima wonse+ ndi kumutonthoza, kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe ndi chisoni chake chopitirira malire.+ 8 Choncho ndikukudandaulirani kuti mumutsimikizire kuti mumamukonda.+ 9 Pakuti ndikulemba zimenezi pofuna kudziwa ngati mulidi omvera m’zinthu zonse.+ 10 Chilichonse chimene mwakhululukira munthu ndi mtima wonse, inenso ndimukhululukira chimodzimodzi.+ Ndipo chilichonse chimene ineyo ndakhululukira munthu ndi mtima wonse, ngati chilipo chimene ndakhululuka ndi mtima wonse, ndachita zimenezo chifukwa cha inuyo, pamaso pa Khristu, 11 kuti Satana asatichenjerere,+ pakuti tikudziwa bwino ziwembu zake.+
12 Nditafika ku Torowa+ kukalengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, ndipo mwayi wina utanditsegukira mu ntchito ya Ambuye,+ 13 mtima wanga sunakhazikike chifukwa Tito+ m’bale wanga sindinamupeze. Ndiye ndinatsanzikana ndi abale kumeneko, n’kupita ku Makedoniya.+
14 Koma tiyamike Mulungu amene nthawi zonse amatitsogolera+ pamodzi ndi Khristu ngati kuti tikuguba pa chionetsero chonyadirira kupambana.+ Kudziwa Mulungu kuli ngati fungo lonunkhira bwino ndipo kudzera mu ntchito yathu fungoli likufalikira paliponse.+ 15 Pakuti pamaso pa Mulungu ndife fungo lonunkhira bwino+ lonena za uthenga wa Khristu, limene likumvedwa ndi anthu amene akupita kukapulumuka komanso ndi amene akupita kukawonongedwa.+ 16 Kwa amene akupita kukawonongedwawo ndife fungo lochokera ku imfa kupita ku imfa,+ koma kwa amene akupita kukapulumukawo ndife fungo lochokera ku moyo kupita ku moyo. Ndipo ndani ali woyenerera kugwira ntchito imeneyi?+ 17 Ifeyo ndife oyenerera. Pakuti mawu a Mulungu sitichita nawo malonda+ ngati mmene ambiri akuchitira,+ koma timalankhula moona mtima monga otsatira Khristu, okhala pamaso pa Mulungu, komanso ngati anthu amene atumidwa ndi Mulungu.+
3 Kodi tikuyambanso kudzichitira umboni tokha?+ Kapena kodi n’kofunika kuti ifenso, mofanana ndi anthu ena, tikhale ndi makalata+ otichitira umboni kwa inu kapena ochokera kwa inu? 2 Inuyo ndiye kalata yathu,+ yolembedwa pamitima yathu, yodziwika ndiponso yowerengedwa ndi anthu onse.+ 3 Pakuti zikuonekeratu kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu yolembedwa ndi ifeyo kudzera mu utumiki wathu.+ Kalatayo siyolembedwa ndi inki koma ndi mzimu+ wa Mulungu wamoyo. Siyolembedwa pazolembapo zamiyala,+ koma zamnofu, pamitima.+
4 Tsopano kudzera mwa Khristu, tikhoza kunena zimenezi molimba mtima+ pamaso pa Mulungu. 5 Sitinganene kuti ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha mphamvu zathu,+ koma ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha Mulungu,+ 6 ndipo chifukwa cha iyeyo ndife oyenera kukhala atumiki a pangano latsopano,+ ndipo ndife ogwirizana osati kudzera m’malamulo olembedwa,+ koma mu mzimu.+ Pakuti malamulo olembedwa amaweruza munthu+ kuti afe, koma mzimu umapatsa munthu moyo.+
7 Ndiponso malamulo amene amapereka imfa,+ amenenso analembedwa pamiyala,+ anabwera ndi ulemerero waukulu kwambiri+ moti ana a Isiraeli sanathe kuyang’anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa inali kuwala ndi ulemerero,+ ulemerero umene unatha patapita nthawi. 8 Chotero, kodi mzimu+ sukuyenera kuperekedwa ndi ulemerero waukulu koposa pamenepa?+ 9 Pakuti ngati malamulo oweruza anthu kuti alangidwe+ anaperekedwa ndi ulemerero,+ chilungamo chikuyenera kuperekedwa+ ndi ulemerero waukulu kuposa pamenepa.+ 10 Nawonso malamulo olembedwa amene anapatsidwa ulemerero poyamba achotsedwa ulemererowo,+ chifukwa ulemerero umene wabwera pambuyo pawo ndi wokulirapo.+ 11 Pakuti ngati malamulo olembedwa, amene anatha patapita nthawi, anaperekedwa ndi ulemerero,+ ndiye kuti okhalapo nthawi zonse adzakhala ndi ulemerero woposa pamenepo.+
12 Chotero popeza tili ndi chiyembekezo chimenechi,+ tikulankhula momasuka kwambiri, 13 osati ngati Mose amene anaphimba nkhope yake ndi nsalu,+ kuti ana a Isiraeli asaone kutha+ kwa ulemerero wosakhalitsawo. 14 Ndipo maganizo awo anachita khungu.+ Pakuti mpaka lero, nsaluyo imakhalabe yophimba powerenga pangano lakale,+ chifukwa imachotsedwa kudzera mwa Khristu basi.+ 15 Moti mpaka lero, pamene zolemba za Mose zikuwerengedwa,+ mitima yawo imakhalabe yophimba.+ 16 Koma munthu akatembenukira kwa Yehova, chophimbacho chimachotsedwa.+ 17 Tsopano Yehova ndiye Mzimu,+ ndipo pamene pali mzimu+ wa Yehova,+ pali ufulu.+ 18 Tonsefe+ tili ndi nkhope zosaphimba ndipo tili ngati magalasi oonera amene amaonetsa ulemerero wa Yehova.+ Pamene tikuonetsa ulemerero umenewu, timasintha+ n’kukhala ngati chifaniziro chake+ ndipo timaonetsa ulemerero wowonjezerekawonjezereka+ mofanana ndendende ndi mmene Yehova, amene ndi Mzimu, watisinthira.+
4 Popeza tili ndi utumiki umenewu+ malinga ndi chifundo chimene tinasonyezedwa,+ sitikubwerera m’mbuyo. 2 Koma tasiya zinthu zochititsa manyazi zochitikira mseri,+ ndipo sitikuyenda mwachinyengo komanso sitikupotoza mawu a Mulungu.+ Koma pamaso pa Mulungu, takhala chitsanzo chabwino kwa chikumbumtima cha munthu aliyense.+ 3 Tsopano ngati uthenga wabwino umene tikulengeza uli wophimbika, ndi wophimbika pakati pa anthu amene akupita kukawonongedwa.+ 4 Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira,+ kuti asaone+ kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero+ wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro+ cha Mulungu. 5 Pakuti sitikulalikira za ifeyo koma za Khristu Yesu, kuti iye ndiye Ambuye+ ndipo ifeyo ndife akapolo+ anu chifukwa cha Yesu. 6 Pakuti Mulungu ndiye anati: “Kuwala kuunike kuchokera mu mdima,”+ ndipo kudzera mwa nkhope ya Khristu,+ waunika mitima yathu kuti iwale+ ndi ulemerero wokhudzana ndi kudziwa+ Mulungu.
7 Komabe, tili ndi chuma+ chimenechi m’zonyamulira+ zoumbidwa ndi dothi,+ kuti mphamvu+ yoposa yachibadwa ichokere kwa Mulungu,+ osati kwa ife.+ 8 Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse,+ koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.+ 9 Timazunzidwa, koma osati mochita kusowa kolowera.+ Timagwetsedwa pansi,+ koma sitiwonongedwa.+ 10 Kulikonse kumene tikupita, timapirira m’matupi mwathu ndipo timakhala pa ngozi yoti tikhoza kuphedwa, ngati mmene Yesu anachitira,+ kuti moyo wa Yesu uonekerenso m’matupi mwathu.+ 11 Pakuti nthawi zonse amoyofe timakhala pa ngozi yoti tikhoza kuphedwa+ chifukwa cha Yesu, kuti moyo wa Yesu uonekerenso m’thupi lathu lokhoza kufali.+ 12 Choncho ngakhale kuti moyo wathu ukukhala pa ngozi, zimenezi zikubweretsa moyo kwa inuyo.+
13 Tsopano, popeza tili ndi mtima wachikhulupiriro wofanana ndi umene anaunena kuti: “Ndinali ndi chikhulupiriro, chotero ndinalankhula,”+ ifenso tili ndi chikhulupiriro, chotero tikulankhula, 14 podziwa kuti amene anaukitsa Yesu adzaukitsanso ifeyo pamodzi ndi Yesu, ndipo adzatipititsa pamaso pa Yesuyo pamodzi ndi inuyo.+ 15 Pakuti zonsezi zachitika chifukwa cha ubwino wanu.+ Ndiponso zachitika kuti kukoma mtima kwakukulu kumene kunawonjezeka kuchulukebe chifukwa cha anthu ambiri amene akupereka mapemphero oyamikira, zimene zikuchititsa kuti Mulungu alandire ulemerero.+
16 Choncho sitikubwerera m’mbuyo. Koma ngakhale munthu wathu wakunja akutha, ndithudi munthu wathu wamkati+ akukhalitsidwanso watsopano tsiku ndi tsiku. 17 Pakuti ngakhale kuti masautso amene tikukumana nawo ndi akanthawi+ ndipo ndi opepuka, masautsowo akutichititsa kuti tilandire ulemerero umene ukukulirakulira komanso wamuyaya,+ 18 pamene tikuika maso athu pa zinthu zosaoneka, osati pa zooneka.+ Pakuti zooneka n’zakanthawi,+ koma zosaoneka n’zamuyaya.+
5 Tikudziwa kuti nyumba yathu ya padziko lapansi pano,+ msasa uno,+ ikadzaphwasuka,+ tidzalandira nyumba yochokera kwa Mulungu. Imeneyo idzakhala nyumba yosamangidwa ndi manja,+ koma yamuyaya,+ ndipo idzakhala kumwamba. 2 Pakuti tikubuula m’nyumba imene tikukhalamoyi+ pofunitsitsa kuvala yathu yakumwamba,+ 3 kuti tikadzaivala, tisadzapezeke amaliseche.+ 4 Ndipotu, ife amene tili mumsasa uno tikubuula chifukwa cholemedwa. Kwenikweni si chifukwa chofuna kuuvula, koma kuti tivale nyumba inayo,+ kuti chokhoza kufachi chilowedwe m’malo ndi moyo.+ 5 Tsopano amene anatikonzekeretsa kuti tilandire zimenezi ndi Mulungu.+ Iye ndiye anatipatsa chikole+ cha zinthu zam’tsogolo, chomwe ndi mzimu.+
6 Chotero nthawi zonse timakhala olimba mtima ndipo tikudziwa kuti pamene tikukhala m’thupi, tili kutali ndi Ambuye,+ 7 pakuti tikuyenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.+ 8 Koma tikulimba mtima ndipo ndife okondwa kukakhala ndi Ambuye, m’malo mokhala m’thupi linoli.+ 9 Choncho n’cholinga chathunso kuti, kaya tikhale ndi iye kapena tikhale kutali naye,+ tikhale ovomerezeka kwa iye.+ 10 Pakuti mtima wa aliyense wa ife udzaonekera pamaso pa mpando woweruzira milandu wa Khristu,+ kuti aliyense alandire mphoto yake pa zinthu zimene anachita ali m’thupi, mogwirizana ndi zimene anali kuchita, zabwino kapena zoipa.+
11 Choncho popeza timaopa+ Ambuye, tikupitiriza kukopa+ anthu. Mulungu akudziwa bwino zolinga zathu. Koma ndili ndi chikhulupiriro kuti inunso, mwachikumbumtima chanu, mukudziwa bwino zolinga zathu.+ 12 Sikuti tayambanso kudzichitira umboni+ tokha kwa inu ayi, koma tikukupatsani chifukwa chodzitamandira, ndipo chifukwacho ndifeyo,+ kuti muwayankhe amene amadzitama chifukwa cha maonekedwe akunja,+ osati chifukwa cha mtima.+ 13 Pakuti ngati tinachita misala,+ tinachitira Mulungu. Ngati tili olongosoka,+ cholinga ndi kupindulitsa inuyo. 14 Pakuti chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse,+ chifukwatu onsewo anali atafa kale. 15 Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha,+ koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera+ n’kuukitsidwa.+
16 Ndiye chifukwa chake kuyambira tsopano sitiona munthu mwakuthupi.+ Ngakhale kuti Khristu tinamuona mwakuthupi,+ tsopano sitikumuonanso motero.+ 17 Choncho ngati aliyense ali wogwirizana ndi Khristu, iye ndi cholengedwa chatsopano.+ Zinthu zakale zinatha,+ ndipo pali zatsopano.+ 18 Koma zinthu zonse n’zochokera kwa Mulungu, amene anatigwirizanitsa+ ndi iyeyo kudzera mwa Khristu, ndipo anatipatsa utumiki+ wokhazikitsanso mtendere. 19 Utumiki wake ndi woti tilengeze kuti Mulungu anali kugwirizanitsa dziko+ ndi iyeyo+ kudzera mwa Khristu,+ moti sanawawerengere anthuwo machimo awo,+ ndipo watipatsa ifeyo ntchito yolengeza uthenga+ umenewu wokhazikitsanso mtendere.+
20 Chotero ndife+ akazembe+ m’malo mwa Khristu,+ ngati kuti Mulungu akuchonderera anthu kudzera mwa ife.+ Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti:+ “Gwirizananinso ndi Mulungu.” 21 Amene analibe uchimoyo,+ Mulungu anamupanga kukhala uchimo+ chifukwa cha ife, kuti tikhale olungama pamaso pa Mulungu+ kudzera mwa iye.
6 Pamene tikugwira naye ntchito limodzi,+ tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.+ 2 Pakuti iye anati: “Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo m’tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.”+ Ndithudi, inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezedwa.+ Linolo ndilo tsiku lachipulumutso.+
3 Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa,+ kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa.+ 4 Koma tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi mwa kupirira zambiri, kudutsa m’masautso, kukhala osowa, kukumana ndi zovuta,+ 5 kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende,+ kukumana ndi zipolowe, kugwira ntchito mwakhama, kusagona tulo, ndi kukhala osadya.+ 6 Tikusonyezanso zimenezi mwa kukhala oyera, odziwa zinthu, oleza mtima,+ okoma mtima,+ okhala ndi mzimu woyera, osonyeza chikondi chopanda chinyengo,+ 7 olankhula zoona, ndiponso okhala ndi mphamvu ya Mulungu.+ Komanso, tikuchita zimenezi ponyamula zida+ za chilungamo kudzanja lamanja ndi lamanzere, 8 mwa kupatsidwa ulemerero ndi kutonzedwa, mwa kuneneredwa zoipa komanso zabwino. Mwa kukhala ngati achinyengo+ koma oona mtima, 9 ngati osadziwika koma odziwika bwino,+ ngati oti tikufa koma tikukhalabe ndi moyo,+ ngati olangidwa+ koma osakaphedwa,+ 10 ngati ogwidwa ndi chisoni koma osangalala nthawi zonse, ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri, ngati opanda kalikonse koma okhala ndi zinthu zonse.+
11 Takhala tikulankhula mosabisa mawu kwa inu Akorinto, tafutukula mtima wathu.+ 12 Malo sakukucheperani mumtima mwathu,+ koma m’chikondi chanu ndi mmene muli malo ochepa.+ 13 Choncho mutibwezere zofanana ndi zimene takuchitirani. Ndikulankhula nanu ngati ana anga,+ inunso futukulani mtima wanu.
14 Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+ 15 Ndiponso pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?*+ Kapena munthu wokhulupirira angagawane+ chiyani ndi wosakhulupirira? 16 Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+ 17 “‘Choncho tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova.* ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’”+ “‘ndipo ndidzakulandirani.’”+ 18 “‘Ndidzakhala atate wanu,+ ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’+ watero Yehova Wamphamvuyonse.”+
7 Chotero okondedwanu, popeza talonjezedwa zinthu zimenezi,+ tiyeni tidziyeretse+ ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu,+ kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.+
2 Tipatseni malo m’mitima mwanu.+ Ifetu sitinalakwire aliyense, sitinaipitse aliyense, ndipo sitinachenjerere aliyense.+ 3 Sikuti ndanena izi kuti ndikutsutseni ngati olakwa ayi. Pajatu ndanena kale kuti inuyo muli m’mitima yathu, kaya tife kapena tikhale moyo.+ 4 Ndimalankhula nanu momasuka kwambiri. Ndimakunyadirani kwambiri.+ Mtima wanga walimbikitsidwa kwambiri,+ ndipo ndikusefukira ndi chimwemwe m’masautso athu onse.+
5 Ndipotu, pamene tinafika ku Makedoniya,+ thupi lathu silinapumule,+ koma masautso amitundumitundu anapitirizabe kutigwera.+ Kunja anali kulimbana nafe, mkati tinali kukhala mwamantha. 6 Komabe Mulungu, amene amalimbikitsa+ osautsika mtima, anatilimbikitsa ndi kukhalapo* kwa Tito. 7 Koma osati chabe chifukwa tinali ndi Tito, komanso chifukwa cha mmene inuyo munamulimbikitsira, pamene anatibweretsera uthenga+ wakuti mukufunitsitsa kulapa, muli ndi chisoni, ndiponso mukundidera nkhawa. Nditamva zimenezi ndinakondweranso kwambiri.
8 Choncho ngakhale kuti ndinakuchititsani kumva chisoni ndi kalata yanga,+ sindikudandaula. (Ndikuona kuti kalatayo inakuchititsani kumva chisoni, koma kwa kanthawi kochepa.) Chotero, ngakhale kuti poyambapo ndinadandaula, 9 panopa ndikukondwera. Sikuti ndikukondwera chifukwa munamva chisoni, koma chifukwa chakuti chisoni chimene munamvacho chinakuchititsani kulapa.+ Pakuti munamva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu,+ chotero simunapwetekedwe m’njira iliyonse chifukwa cha zimene tinalemba. 10 Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa ndi kupeza chipulumutso, zimene munthu sangadandaule nazo.+ Koma chisoni cha dziko chimabweretsa imfa.+ 11 Ndipo taonani zimene chisoni chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu+ chimenechi chakuchitirani. Chakuchititsani kukhala akhama kwambiri, chakuchititsani kudziyeretsa, kuipidwa, mantha, kufunitsitsa kulapa, kudzipereka, ndiponso kukonza cholakwacho.+ Mwanjira ina iliyonse, munasonyeza kuti ndinu oyera pa nkhani imeneyi. 12 Ndithudi, ngakhale kuti ndinakulemberani, sindinatero chifukwa cha wolakwayo+ kapena wolakwiridwayo ayi, koma kuti khama lanu lofuna kumvera mawu athu lionekere pamaso pa Mulungu. 13 N’chifukwa chake talimbikitsidwa.
Komabe, kuwonjezera pa kulimbikitsidwa, tinakondweranso kwambiri chifukwa chakuti Tito ali ndi chimwemwe, popeza nonsenu mwatsitsimutsa mtima wake.+ 14 Pakuti ngati ndinalankhula mokunyadirani kwa iyeyo, simunandichititse manyazi. Koma zimene tinalankhula monyadira kwa Tito n’zoona,+ monganso mmene zilili zinthu zonse zimene tinalankhula nanu. 15 Ndiponso iyeyo amakukondani kwambiri nonsenu akakumbukira kumvera kwanu,+ komanso mmene munamulandirira ndi mantha ndiponso kunjenjemera. 16 Ndine wosangalala kuti m’njira iliyonse mukundilimbikitsa.+
8 Tsopano abale, tikufuna kukudziwitsani za kukoma mtima kwakukulu kumene mipingo ya ku Makedoniya yasonyezedwa ndi Mulungu.+ 2 Pamene iwo anali kuyesedwa kwambiri chifukwa cha mavuto, anali achimwemwe kwambiri ndiponso anasonyeza kuwolowa manja kwakukulu, ndipo anachita zimenezi ngakhale kuti anali pa umphawi wadzaoneni.+ 3 Pakuti anachita malinga ndi zimene akanatha,+ komanso ndikuwachitira umboni kuti anachita ngakhale zoposa pamenepo, 4 ndipo anapitiriza kutipempha mochokera pansi pa mtima ndiponso mochonderera kwambiri, kuti tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso zachifundo ndi kutinso achite nawo utumiki wothandiza oyerawo.+ 5 Ndipo iwo sanangochita zimene tinali kuyembekeza zokha, koma choyamba anadzipereka kwa Ambuye+ ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu. 6 Zimenezi zinatichititsa kuti timulimbikitse Tito+ kuti, popeza iye ndiye anayambitsa zoperekazi pakati panu, iyeyo amalizitse kusonkhanitsa mphatso zanu zachifundo. 7 Inuyo mukusefukira mu ntchito+ monga chikhulupiriro, kudziwa kulankhula, kudziwa zinthu,+ khama pa zonse zimene mumachita, ndipo mumasonyeza chikondi chofanana ndi chimene tili nacho pa inu. Chotero musefukirenso chimodzimodzi pa nkhani ya kupereka kumene tikunenaku.
8 Sindikukulamulani,+ koma ndikulankhula izi chifukwa cha khama limene ena asonyeza, kutinso ndione ngati chikondi chanu chilidi chenicheni. 9 Pakuti mukudziwa kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti ngakhale kuti iye anali wolemera, anakhala wosauka chifukwa cha inu,+ kuti inuyo mulemere+ kudzera m’kusauka kwake.
10 Ndipereke maganizo anga pamenepa:+ nkhani imeneyi ndi yopindulitsa kwa inu,+ poona kuti chaka chimodzi chatha kale kuyambira pamene munayambitsa zimenezi. Sikuti munangoziyambitsa chabe, komanso munazichita modzipereka kwambiri.+ 11 Ndiyeno tsopano, malizitsani kupatsa kumeneku, kuti monga mmene munalili ofunitsitsa kuchita zimenezi, mumalizitsenso kutero malinga ndi zimene muli nazo. 12 Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe,+ osati zimene sangathe. 13 Sindikufuna kuti kwa ena zikhale zosavuta,+ koma kwa inu zovuta ayi. 14 Koma ndikufuna kuti zochuluka zimene muli nazo zithandizire pa zimene iwowo akusowa, ndipo zochuluka zimene iwowo ali nazo zithandizire pa zimene inuyo mukusowa, kuti pakhale kufanana.+ 15 Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Munthu wokhala ndi zambiri sanakhale ndi zopitirira muyezo, ndipo munthu wokhala ndi zochepa sanakhale ndi zocheperatu.”+
16 Tikuyamika Mulungu chifukwa Tito amakuderaninso nkhawa ngati mmene ifeyo timachitira,+ 17 chifukwa iyeyo wamveradi zimene tinamulimbikitsa kuti achite, ndipo popeza kuti ndi wakhama kwambiri, akubwera kwanuko mwa kufuna kwake. 18 Komanso pamodzi ndi iye, tikutumiza m’bale wina amene akutamandidwa m’mipingo yonse chifukwa cha zimene akuchita zokhudzana ndi uthenga wabwino. 19 Si zokhazo, koma anaikidwanso+ ndi mipingo kuti akhale woyenda nafe pamene tikubweretsa mphatso zachifundozi. Tikupereka mphatsozi kuti zipereke ulemerero+ kwa Ambuye, komanso kuti tisonyeze kuti ndife ofunitsitsa kuthandiza ena.+ 20 Choncho sitikufuna kuti munthu aliyense atipeze chifukwa+ pa zopereka zaufulu+ zimene tikubweretsazi. 21 Pakuti “timasamalira zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.”+
22 Pamodzi ndi abalewo, tatumizanso m’bale wathu amene mobwerezabwereza tamuona kuti ndi wakhama pa zinthu zambiri, ndipo tsopano wawonjezera khama lake chifukwa akukukhulupirirani kwambiri. 23 Koma ngati mukukayikira zilizonse zokhudza Tito, ndikufuna ndikuuzeni kuti iye ndi mnzanga komanso ndikugwira naye ntchito limodzi+ pothandiza inuyo. Kapena ngati mungakayikire zilizonse zokhudza abale athuwa, iwo ndi nthumwi za mipingo ndipo amabweretsa ulemerero kwa Khristu. 24 Choncho asonyezeni kuti chikondi+ chanu ndi chenicheni ndiponso kuti sitinakunyadireni pachabe.+
9 Tsopano ponena za utumiki+ wothandiza oyerawo, n’zosafuna kuti ndichite kukulemberani. 2 Pakuti ndikudziwa kuti muli ndi mtima wofunitsitsa ndipo ndikunena zimenezi monyadira kwa Amakedoniya. Ndikumawauza kuti, “Abale a ku Akaya akhala okonzeka kwa chaka chimodzi tsopano,”+ ndipo kudzipereka kwanu kwalimbikitsa ambiri a iwo. 3 Koma ndikutumiza abale kuti tisangokunyadirani pachabe pa nkhani imeneyi, koma kuti mukhaledi okonzeka,+ monga ndinali kuwauzira kuti mudzakhala okonzeka. 4 Koma ngati ndingadzafike kumeneko pamodzi ndi Amakedoniya n’kupeza kuti simuli okonzeka, manyazi adzagwira ifeyo ndi inu nomwe, chifukwa tinali kukudalirani. 5 N’chifukwa chake ndinaona kuti ndi bwino kuti ndilimbikitse abale abwere kwa inu ife tisanafike, n’cholinga choti adzakuthandizeni kukonzeratu mphatso imene mukuipereka chifukwa cha kuwolowa manja kwanu, imenenso munalonjeza pa chiyambi.+ Ndiye tikadzafika, mphatsoyi idzakhala itakonzedwa kale ndipo zidzaonekeratu kuti simukupereka mphatsoyi chifukwa choti takukakamizani, koma chifukwa choti ndinu owolowa manja.+
6 Koma ponena za nkhaniyi, wobzala moumira+ adzakololanso zochepa, ndipo wobzala mowolowa manja+ adzakololanso zochuluka. 7 Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika+ kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.+
8 Komanso, Mulungu akhoza kuchititsa kuti kukoma mtima kwake konse kwakukulu kusefukire kwa inu. Choncho nthawi zonse mudzakhala ndi zinthu zokwanira kusamalira zosowa zanu, ndipo mudzakhalanso ndi zinthu zambiri zogwiritsa ntchito pa ntchito iliyonse yabwino.+ 9 (Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Iye wagawira ena mowolowa manja. Wapereka kwa anthu aumphawi, ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.”+ 10 Tsopano amene amapereka mbewu kwa wobzala, amenenso amapereka chakudya kuti anthu adye,+ adzakupatsani mbewu zoti mubzale ndipo adzakupatsani zimenezi mowolowa manja. Adzawonjezeranso zipatso za chilungamo chanu.)+ 11 Mulungu akukudalitsani m’njira iliyonse kuti muthe kupereka mowolowa manja m’njira zosiyanasiyana, ndipo kudzera m’zochita zathu, kuwolowa manja koteroko kukuchititsa anthu kuyamika Mulunguyo.+ 12 Zili choncho chifukwa utumiki wothandiza anthu umenewu si kuti ukungopatsa oyerawo zinthu zochuluka zimene akufunikira,+ koma ukuchititsanso anthu ambiri kupereka mapemphero ochuluka oyamika Mulungu. 13 Chifukwa cha umboni umene utumikiwu ukupereka, iwo akulemekeza Mulungu. Akutero chifukwa inuyo mwagonjera uthenga wabwino wonena za Khristu,+ monga mmene mukulengezera poyera, ndiponso chifukwa chakuti mwapereka chopereka kwa iwowo ndi kwa onse mowolowa manja.+ 14 Chotero iwo amakuperekerani mapembedzero kwa Mulungu ndiponso amakukondani kwambiri chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu+ kumene Mulungu wakusonyezani.
15 Tikuyamika Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.+
10 Tsopano ineyo Paulo, ndikukudandaulirani mwa kufatsa+ ndi kukoma mtima+ kwa Khristu, ngakhale kuti ndimaoneka wosanunkha kanthu+ ndikakhala pakati panu, koma wolimba mtima polankhula nanu ndili kwina.+ 2 Ndithu ndikanakonda kuti anthu amene akuona kuti ifeyo timachita zinthu motsatira maganizo a dzikoli,* asinthe maganizo awo, kuti ndikadzabwera kumeneko ndisadzachite zinthu zazikulu zotsutsana nawo.+ 3 Pakuti ngakhale kuti moyo wathu ndi wofanana ndi wa anthu ena onse,+ sitikumenya nkhondo motsatira maganizo a dzikoli.+ 4 Pakuti zida za nkhondo yathu si zochokera m’dziko lino,+ koma ndi zida zamphamvu zimene Mulungu watipatsa,+ zimene zimatha kugwetsa zinthu zozikika molimba. 5 Pakuti tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu,+ ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvera Khristu. 6 Komanso ndife okonzeka kupereka chilango pa aliyense wosamvera,+ inuyo mukadzasonyeza kuti ndinu omvera pa chilichonse.+
7 Mukuona zinthu mogwirizana ndi maonekedwe ake akunja.+ Ngati aliyense amakhulupirira mumtima mwake kuti ndi wotsatira Khristu, adziwenso kuti, monga mmene iye alili wotsatira Khristu, ifenso ndife otsatira Khristu.+ 8 Pakuti ngakhale nditati ndidzitamandire+ mopitirirako muyezo za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa kuti tikulimbikitseni, osati kukupasulani,+ sindingachite manyazi. 9 Ponena zimenezi, sindikufuna kuti muganize kuti makalata anga cholinga chake n’kukuopsezani. 10 Pakuti ena amati: “Makalata ake ndi olemerera ndi amphamvu, koma iyeyo akakhala pakati pathu amaoneka wofooka+ ndipo nkhani zake n’zosagwira mtima.”+ 11 Munthu woteroyo adziwe kuti zimene tikunena m’makalata athu tili kwina, tidzachitanso zomwezo tikadzakhala pakati panu.+ 12 Pakuti sitidzayesa n’komwe kudziona ngati ndife ofanana ndi anthu enaake kapena kudziyerekezera ndi ena amene amadzikweza.+ Ndithudi anthu amenewo samvetsa kanthu kalikonse chifukwa akuyezana okhaokha pogwiritsira ntchito miyezo yawo yomwe, ndipo akudziyerekezera ndi iwo eni.+
13 Koma ifeyo tidzadzitamandira, osati pa zinthu zimene zili kunja kwa malire amene tapatsidwa,+ koma pa zinthu zimene zili mkati mwa malire a gawo limene Mulungu anatipatsa pochita kutiyezera, limene analifikitsa mpaka kwanuko.+ 14 Choncho sitikupitirira malire a gawo lathu, ngati kuti gawolo silikufika kwa inu. Ayi ndithu, pakuti tinayamba ndife kufika kwanuko polengeza uthenga wabwino wonena za Khristu.+ 15 Sitikudzitamandira kunja kwa malire a gawo limene tinapatsidwa, podzitamandira chifukwa cha ntchito za munthu wina ayi,+ koma tili ndi chiyembekezo chakuti chikhulupiriro chanu chikadzawonjezeka,+ ntchito yathunso idzakula pakati panu, limene ndi gawo lathu.+ Ndiyeno tidzachitanso zowonjezereka, 16 polengeza uthenga wabwino kumayiko akutali kupitirira kwanuko,+ kuti tisadzitamande m’gawo la wina, mmene anakonzamo kale. 17 “Koma amene akudzitamandira, adzitamande mwa Yehova.”+ 18 Pakuti wodzikweza yekha si amene amavomerezedwa,+ koma amene Yehova+ wamuvomereza.+
11 Ndikanakonda kuti mundilole kuti ndidzikweze pang’ono.+ Ndipotu zoona zake n’zakuti, mwandilola kale. 2 Ndikukuchitirani nsanje,+ ngati imene Mulungu amakuchitirani, popeza ndine ndinakuchititsani kulonjezedwa ukwati+ ndi mwamuna mmodzi,+ Khristu,+ ndipo ndikufuna kukuperekani ngati namwali woyera+ kwa iye. 3 Koma nkhawa yanga ndi yakuti mwina, monga mmene njoka inanamizira Hava+ ndi chinyengo chake, maganizo anunso angapotozedwe+ kuti musakhalenso oona mtima ndi oyera ngati mmene muyenera kuchitira kwa Khristu.+ 4 Chifukwa panopa wina akabwera kwa inu n’kulalikira za Yesu wosiyana ndi amene tinamulalikira,+ kapena wina akakubweretserani mzimu wosiyana ndi umene munalandira kale,+ kapena uthenga wabwino+ wosiyana ndi umene munaulandira, inu mumangomulolera munthu woteroyo.+ 5 Koma ine ndikuona kuti sindikuchepa+ mwanjira ina iliyonse kwa atumwi anu apamwambawo.+ 6 Ngati ndilibe luso la kulankhula,+ si kuti ndine wosadziwanso zinthu.+ Koma m’njira iliyonse tinakusonyezani kuti ndife odziwa zinthu pa zonse.+
7 Kapena kodi ndinachita tchimo pamene ndinadzichepetsa+ kuti inuyo mukwezedwe, muja ndinalengeza mosangalala uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu, popanda inuyo kutayirapo ndalama?+ 8 Ndinalanda mipingo ina zinthu zawo polandira chithandizo chawo kuti nditumikire inuyo.+ 9 Koma pamene ndinasowa zofunika zina ndili kwanuko, sindinalemetse ngakhale munthu mmodzi,+ popeza abale amene anachokera ku Makedoniya+ anandipatsa zonse zimene ndinali kuzisowa. Ndithu, sindinakulemetseni m’njira iliyonse, ndipo ndipitirizabe kutero.+ 10 Ndikulankhula choonadi+ cha Khristu, choncho palibe angandiletse kudzitamandira+ m’madera a ku Akaya. 11 Kodi ndachita zimenezi chifukwa chiyani? Chifukwa sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani.+
12 Tsopano ndipitiriza kuchita zimene ndikuchita,+ kuti nditsekereze anthu amene akuyesayesa kupeza chifukwa choti anamizire kuti ndi ofanana ndi ife, podzitamandira chifukwa cha udindo wawo. 13 Pakuti amuna oterowo ndi atumwi onama, antchito achinyengo,+ odzisandutsa atumwi a Khristu.+ 14 Ndipo zimenezo n’zosadabwitsa, popeza ngakhale Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.+ 15 Choncho n’zosadabwitsa ngati atumiki ake+ nawonso amadzisandutsa atumiki a chilungamo. Koma mapeto awo adzakhala monga mwa ntchito zawo.+
16 Ndikubwerezanso kunena kuti, munthu asandiyese wodzikweza. Koma ngati mukundionabe motero, ndilandirenibe monga wodzikweza yemweyo, kuti nanenso ndidzitame pang’ono.+ 17 Zimene ndikulankhulazi, ndikulankhula ngati mmene amalankhulira anthu odzitama ndiponso odzidalira kwambiri. Sindikulankhula motsatira chitsanzo cha Ambuye ayi, koma ngati mmene amalankhulira anthu opanda nzeru.+ 18 Popeza anthu ambiri akudzitama pa zinthu za m’dzikoli,+ inenso ndidzitama. 19 Pakuti mumalolera mosangalala anthu odzikweza, chifukwa mumadziona kuti ndinu ololera. 20 Ndipo mumalolera aliyense wokumangani ukapolo,+ womeza zimene muli nazo, wokulandani zimene muli nazo, wodzikweza pa inu, ndiponso aliyense wokuwombani mbama.+
21 Ndikunena zimenezi mopeputsa ifeyo, ngati kuti ndife ofooka.
Koma ngati wina aliyense akuchita chinachake molimba mtima, ndikulankhula ngati wodzitama,+ inenso ndikuchita chinthu chomwecho molimba mtima. 22 Kodi iwo ndi Aheberi? Inenso ndine Mheberi.+ Kodi ndi Aisiraeli? Inenso ndine Mwisiraeli. Kapena iwo ndi mbewu ya Abulahamu? Inenso chimodzimodzi.+ 23 Ndi atumiki a Khristu kapena? Ndikuyankha ngati wamisala, ineyo ndiye weniweni woposanso iwowo:+ m’ntchito zovuta mowirikiza koposa,+ m’ndende osachita kunena,+ kumenyedwa kosawerengeka, kutsala pang’ono kufa kawirikawiri.+ 24 Kasanu Ayuda anandikwapula zikoti 40+ kuchotsera chimodzi. 25 Katatu anandimenya ndi ndodo.+ Kamodzi anandiponya miyala.+ Chombo chinandiswekerapo katatu.+ Kamodzi ndinakhala pamadzi akuya usiku ndi usana wonse. 26 Pa maulendo kawirikawiri, zoopsa za m’mitsinje, zoopsa za achifwamba pamsewu,+ zoopsa zochokera kwa anthu a mtundu wanga,+ zoopsa zochokera kwa anthu a mitundu ina,+ zoopsa mumzinda,+ zoopsa m’chipululu, zoopsa za panyanja, zoopsa pakati pa abale onyenga, 27 m’ntchito yolimba ndi m’thukuta, kawirikawiri osagona tulo usiku,+ njala ndi ludzu,+ nthawi zambiri osadya chakudya,+ kuzizidwa ndi kukhala wosavala.
28 Kuwonjezera pa zinthu za kunja kwa thupi zimenezo, palinso chimene chimandivutitsa maganizo tsiku ndi tsiku, ndicho nkhawa imene ndimakhala nayo pa mipingo yonse.+ 29 Ndani ali wofooka,+ ine osakhalanso wofooka? Ndani wakhumudwitsidwa, ine osakwiya nazo?
30 Ngati ndiyenera kudzitama, ndidzadzitama+ pa zinthu zokhudza kufooka kwanga. 31 Mulungu ndi Atate wa Ambuye Yesu, amene ali woyenera kutamandidwa kwamuyaya, akudziwa kuti sindikunama. 32 Ku Damasiko, bwanamkubwa wa mfumu Areta anali kulondera mzinda wa Adamasiko kuti andigwire,+ 33 koma ndinaikidwa m’dengu n’kutsitsidwa pawindo la mpanda wa mzindawo,+ ndipo ndinapulumuka m’manja mwake.
12 Ndiyenera kudzitama. Zoona, kudzitama si kopindulitsa. Koma tiyeni tisiye kaye nkhani imeneyi, tipite ku nkhani yokhudza masomphenya+ ndi mauthenga ochokera kwa Ambuye. 2 Ndikudziwa munthu wina wogwirizana ndi Khristu. Zaka 14 zapitazo, munthu ameneyu anakwatulidwira kumwamba kwachitatu. Kaya zimenezo zinachitika ali m’thupi kapena ali kunja kwa thupi sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu.+ 3 Zoonadi, ndikumudziwa munthu ameneyu. Kaya anakwatulidwa ali m’thupi kapena kunja kwa thupi,+ sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu. 4 Iye anakwatulidwa n’kukalowa m’paradaiso,+ ndipo ali m’paradaisomo anamva mawu osatchulika, amene sikololeka munthu kuwanena. 5 Ndidzadzitamandira chifukwa cha munthu ameneyo, koma sindidzadzitamandira chifukwa cha ineyo, kupatulapo pa kufooka kwanga.+ 6 Ngati ndingafune kudzitamandira, si kuti ndikhala wodzikweza,+ chifukwa ndikhala ndikunena choonadi. Koma sindikudzitamandira, chifukwa ndikufuna kuti inuyo mundiyamikire pa zinthu zokhazo zimene mukuona kapena kumva kwa ine. 7 Chifukwa cha kuchuluka kwa mauthenga amene anaululidwa kwa ine, aliyense asandiganizire koposa mmene ayenera kundiganizira.
Chotero, kuti ndisadzikweze mopitirira muyezo,+ ndinapatsidwa munga m’thupi,+ mngelo wa Satana woti azindimenya nthawi zonse, kuti ndisadzikweze mopitirira muyezo. 8 Pa nkhaniyi, katatu+ konse ndinachonderera Ambuye kuti mungawu undichoke, 9 koma anandiuza motsimikiza kuti: “Kukoma mtima kwakukulu kumene ndakusonyeza n’kokukwanira,+ pakuti mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.”+ Choncho, ndidzadzitamandira mosangalala kwambiri pa kufooka kwanga,+ kuti mphamvu ya Khristu ikhalebe pamutu panga ngati hema. 10 Chotero ndimasangalala ndi kufooka, zitonzo, zosowa zanga, mazunzo ndi zovuta zina, chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.+
11 Ndakhala wodzikweza tsopano. Ndinu mwandikakamiza+ kukhala wotero, popeza simunanene za zinthu zabwino zimene ndachita, ngakhale kuti munayenera kutero. Pakuti sindinachepe mwanjira ina iliyonse kwa atumwi anu apamwambawo,+ ngakhale kuti si ine kanthu m’maso mwanu.+ 12 Ndithudi inuyo munaona umboni wakuti ndine mtumwi,+ poona mmene ndinapiririra,+ komanso poona zizindikiro, zodabwitsa, ndi ntchito zamphamvu zimene ndinachita.+ 13 Kodi munakhala ochepa m’njira yotani kwa mipingo yonse? Mwina m’njira yoti ineyo sindinakhale katundu wolemetsa kwa inu.+ Chonde, ndikhululukireni cholakwa chimenechi.
14 Kanotu ndi kachitatu+ kukhala wokonzeka kubwera kwa inu, koma sindidzakhala katundu wolemetsa. Pakuti sindikufuna zinthu zanu,+ koma inuyo. Paja ana+ sayenera kusunga chuma kuti chidzathandize makolo awo m’tsogolo, koma makolo ndi amene ayenera kusungira ana awo.+ 15 Koma ineyo ndidzagwiritsa ntchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipereka ndi moyo wanga wonse chifukwa cha miyoyo yanu.+ Ngati ineyo ndimakukondani kwambiri chonchi, kodi inuyo mukuyenera kundikonda mochepa? 16 Mulimonse mmene zinakhalira, sindinakulemetseni.+ Ngakhale zili choncho, inuyo mukuti, “ndinakuchenjererani” ndi kukukolani “mwachinyengo.”+ 17 Koma sindinakuchenjerereni kudzera mwa aliyense wa anthu amene ndinawatumiza kwa inu, ndinatero ngati? 18 Tito ndinamuchonderera kuti abwere kwa inu ndipo ndinatumiza m’bale wina limodzi naye. Kodi Titoyo anakuchenjererani m’pang’ono pomwe ngati?+ Ayi ndithu sanatero. Tinayenda mumzimu umodzi,+ kodi si choncho? M’mapazi amodzimodzi, si choncho kodi?
19 Kodi nthawi yonseyi mwakhala mukuganiza kuti tikudzitchinjiriza pamaso panu? Tikulankhula pamaso pa Mulungu mogwirizana ndi Khristu. Komatu okondedwa, tikuchita zonse kuti tikulimbikitseni.+ 20 Ndikuopa kuti mwinamwake ndikadzafika,+ sindidzakupezani mmene ndikanafunira. Kwa inunso sindidzakhala mmene mukanafunira. M’malomwake, ndidzapeza ndewu, nsanje,+ kukwiyitsana, mikangano, miseche, manong’onong’o, kudzitukumula, ndi zisokonezo.+ 21 Mwina ndikadzabweranso, Mulungu wanga adzandichititsa manyazi pakati panu. Ndipo mwina ndidzalirira anthu ambiri amene anachimwa+ koma sanalape pa zonyansa zawo, dama*+ lawo, ndi khalidwe lawo lotayirira+ limene akhala akuchita.
13 Aka ndi kachitatu+ tsopano kukonza ulendo wobwera kwanuko. “Muzitsimikizira nkhani iliyonse mutamva umboni wa pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.”+ 2 Ngakhale kuti panopa ndili kutali ndi inu, koma muone mawu angawa ngati kuti ndili limodzi nanu kachiwiri. Choncho, monga mmene ndinachitira kale, ndikuchenjeza anthu amene anachimwa, komanso ena onse, kuti ndikadzabweranso kumeneko sindidzalekerera munthu.+ 3 Ndatero chifukwa mukufunafuna umboni wosonyeza kuti Khristu akulankhuladi mwa ine.+ Iye si wofooka kwa inu koma ndi wamphamvu pakati panu. 4 Zoonadi, iye anapachikidwa pamtengo+ chifukwa anadzakhala wofooka,+ koma ali ndi moyo mwa mphamvu ya Mulungu.+ Inde, ifenso ndife ofooka limodzi naye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye+ mwa mphamvu ya Mulungu+ imene ikugwira ntchito mwa inu.
5 Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.+ Kodi simukudziwa kuti Yesu Khristu ndi wogwirizana ndi inu?+ Muyenera kudziwa zimenezi, kupatulapo ngati muli osavomerezeka. 6 Ndikukhulupirira kuti mudzadziwa kuti ndife ovomerezeka.
7 Tsopano tikupemphera+ kwa Mulungu kuti musachite cholakwa chilichonse. Cholinga changa pochita zimenezi si chakuti ifeyo tioneke kuti ndife ovomerezeka ayi, koma kuti inuyo muzichita zabwino. 8 Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma zinthu zokhazo zogwirizana ndi choonadi.+ 9 Ndithudi timasangalala nthawi zonse inu mukakhala amphamvu, pamene ife tili ofooka.+ Ndipo chimene tikupempherera+ n’chakuti musinthe zinthu zimene mukuyenera kusintha. 10 N’chifukwa chake ndikulemba zinthu zimenezi pamene sindili kumeneko, kuti ndikadzakhalako ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwamphamvu,+ chifukwa Ambuye anandipatsa ulamulirowu kuti ndizikulimbikitsani,+ osati kukufooketsani.
11 Pomalizira abale, ndikuti pitirizani kukondwera, kusintha maganizo anu, kulimbikitsidwa,+ kukhala ndi maganizo ogwirizana,+ ndiponso kukhala mwamtendere.+ Mukatero, Mulungu wachikondi ndi wamtendere+ adzakhala nanu. 12 Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwaubale.+ 13 Oyera onse akupereka moni kwa inu.
14 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu, chikondi cha Mulungu, komanso mzimu woyera umene mukupindula nawo limodzi, zikhale nanu nonsenu.+
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza kuti, “Wopanda pake,” amene ndi woipayo, Satana.
Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 8.
Mawu ake enieni, “mwakuthupi.”
Onani Zakumapeto 7.