Maliro
א [ʼAʹleph]
3 Ine ndine mwamuna wamphamvu amene ndaona masautso+ chifukwa cha ndodo ya ukali wa Mulungu.
2 Iye wanditsogolera ndi kundiyendetsa m’malo amdima, osati m’malo owala.+
3 Ndithudi, iye amandimenya ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.+
ב [Behth]
4 Wafooketsa thupi langa ndipo wachititsa khungu langa kunyala.+ Iye waphwanyanso mafupa anga.+
5 Wandimangira mpanda+ kuti chomera chakupha+ ndi mavuto zindizungulire.
6 Wandichititsa kukhala m’malo amdima,+ ngati munthu woti anafa kalekale.+
ג [Giʹmel]
7 Wanditsekereza ngati mmene mpanda wamiyala umatsekerezera, kuti ndisatuluke.+ Wandimanga ndi maunyolo olemera amkuwa.+
8 Komanso ndikalira ndi kupempha thandizo mofuula, iye amatsekereza pemphero+ langa.
9 Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema.+ Wachititsa njira zanga kukhala zovuta kuyendamo.+
ד [Daʹleth]
10 Kwa ine, iye ali ngati chimbalangondo chimene chandibisalira,+ ndiponso ngati mkango umene wakhala pamalo obisika.+
11 Wasokoneza njira zanga ndipo wandichititsa kukhala wopanda chochita. Wandichititsanso kukhala wosiyidwa.+
12 Wakunga uta wake+ ndipo wandisandutsa chinthu cholasapo mivi+ yake.
ה [Heʼ]
13 Walasa impso zanga ndi mivi yotuluka m’kachikwama kake.+
14 Ndakhala chinthu choseketsa+ kwa anthu onse odana nane, ndipo amandiimba m’nyimbo yawo tsiku lonse.+
15 Wandipatsa zinthu zowawa zokwanira.+ Wandikhutitsa chitsamba chowawa.+
ו [Waw]
16 Wachititsa kuti mano anga aguluke ndi miyala.+ Wandipondaponda m’phulusa.+
17 Inu mwanditayira kutali, moti sindilinso pa mtendere. Sindikukumbukiranso zinthu zabwino.+
18 Nthawi zonse ndikunena kuti: “Ulemerero wanga ndi chiyembekezo changa mwa Yehova zatha.”+
ז [Zaʹyin]
19 Kumbukirani kuti ndine wosautsika ndi wosowa pokhala.+ Kumbukiraninso kuti ndimadya chitsamba chowawa ndi chomera chakupha.+
20 Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.+
21 Ndidzakumbukira zimenezi mumtima mwanga.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima wodikira.+
ח [Chehth]
22 Chifukwa cha kukoma mtima kosatha+ kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe,+ ndipo chifundo chake sichidzatha.+
23 Chifundocho chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse,+ pakuti inu ndinu wokhulupirika kwambiri.+
24 Ine ndanena kuti: “Yehova ndiye cholowa changa.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima womudikira.”+
ט [Tehth]
25 Yehova ndi wabwino kwa munthu amene akumuyembekezera,+ kwa munthu amene akumufunafuna.+
26 Ndi bwino kuti munthu ayembekezere+ chipulumutso cha Yehova+ moleza mtima.+
27 Ndi bwino kuti mwamuna wamphamvu anyamule goli ali mnyamata.+
י [Yohdh]
28 Iye akhale payekha ndipo akhale chete,+ chifukwa Mulungu walola kuti zimenezi zimuchitikire.+
29 Iye awerame mpaka pakamwa pake pafike padothi.+ Mwina angakhale ndi chiyembekezo.+
30 Aperekere tsaya lake kwa munthu amene akumumenya.+ Alandire chitonzo chokwanira.+
כ [Kaph]
31 Pakuti Yehova sadzatitaya mpaka kalekale.*+
32 Ngakhale kuti watichititsa kumva chisoni,+ ndithu adzatichitira chifundo chifukwa kukoma mtima kwake kosatha n’kwakukulu.+
33 Pakuti iye sasangalala ndi kusautsa anthu kapena kuwamvetsa chisoni.+
ל [Laʹmedh]
34 Pajatu kupondaponda+ akaidi onse a padziko lapansi,+
35 Kukankhira pambali chilungamo cha mwamuna wamphamvu pamaso pa Wam’mwambamwamba,+
36 Ndi kupotoza chiweruzo cha munthu pa mlandu wake, Yehova savomereza zimenezi.+
מ [Mem]
37 Tsopano ndani ananenapo kuti chinthu chichitike, chinthucho n’kuchitikadi Yehova asanalamule?+
38 Zinthu zoipa ndi zabwino sizitulukira limodzi pakamwa pa Wam’mwambamwamba.+
39 Kodi munthu angadandaulirenji+ chifukwa cha zotsatirapo za tchimo lake?+
נ [Nun]
40 Tiyeni tifufuze njira zathu kuti tizidziwe,+ ndipo tibwerere kwa Yehova.+
41 Tiyeni tichonderere Mulungu kumwamba ndi mtima wonse, ndipo tikweze manja athu m’mwamba+ ndi kunena kuti:
42 “Ife taphwanya malamulo. Tachita zinthu zopanduka+ ndipo inu simunatikhululukire.+
ס [Saʹmekh]
43 Mwadzitchinga ndi mkwiyo wanu kuti tisakufikireni+ ndipo mukupitiriza kutithamangitsa.+ Mwapha anthu mopanda chisoni.+
44 Mwadzitchinga ndi mtambo waukulu+ kuti pemphero lisadutse ndi kufika kwa inu.+
45 Mwatisandutsa nyansi ndi zinyalala pakati pa anthu a mitundu ina.”+
פ [Peʼ]
46 Pakamwa pa adani athu onse pakutinenera zoipa.+
47 Ife tagwidwa ndi mantha ndipo tikusowa chochita.+ Tasiyidwa ndipo tawonongedwa.+
48 Maso anga akungotuluka misozi ngati mtsinje chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+
ע [ʽAʹyin]
49 Maso anga akungotuluka misozi mosalekeza,+
50 Kufikira Yehova atayang’ana pansi ndi kutiona ali kumwamba.+
51 Mtima wanga ukusautsika ndi zimene maso anga aona,+ zimene zachitikira ana onse aakazi a mzinda wanga.*+
צ [Tsa·dhehʹ]
52 Adani anga akundisaka ngati mbalame+ popanda chifukwa.+
53 Anali kufuna kuchotsa moyo wanga kuti andiponye m’dzenje+ ndipo anali kundiponya miyala.
54 Madzi asefukira ndi kumiza mutu wanga,+ moti ndanena kuti: “Ndifa basi!”+
ק [Qohph]
55 Inu Yehova, ndaitana dzina lanu mofuula ndili m’dzenje lakuya kwambiri.+
56 Mumve mawu anga.+ Musatseke khutu lanu pamene ndikupempha mpumulo ndiponso pamene ndikulirira thandizo.+
57 Pa tsiku limene ndinakuitanani,+ munandiyandikira ndi kundiuza kuti: “Usaope.”+
ר [Rehsh]
58 Inu Yehova, mwandiweruzira milandu yanga.+ Mwawombola moyo wanga.+
59 Inu Yehova, mwaona zoipa zimene andichitira.+ Chonde, ndiweruzireni mlandu wanga.+
60 Mwaona mtima wawo wokonda kubwezera ndiponso ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+
ש [Sin] kapena [Shin]
61 Inu Yehova, mwamva mawu awo otonza ndipo mwaona ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+
62 Mwamva mawu ochokera pakamwa pa anthu amene akundiukira.+ Mwamvanso zoipa zimene akundinenera monong’ona tsiku lonse.+
63 Onani zochita zawo zonse.+ Iwo akundiimba m’nyimbo yawo.+
ת [Taw]
64 Inu Yehova, mudzawabwezera mogwirizana ndi ntchito za manja awo.+
65 Mudzaumitsa mtima wawo,+ ndipo kuchita zimenezi n’kuwatemberera.+
66 Inu Yehova, mudzawakwiyira ndi kuwathamangitsa ndipo mudzawafafaniza+ padziko lanu lapansi.+