Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 25
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Machitidwe 25:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 24:27
  • +Mac 21:15

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 196

Machitidwe 25:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 24:1; 25:15

Machitidwe 25:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 37:32; Miy 1:16; Mac 9:23; 14:5; 23:21; 2Ak 11:26

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 196

Machitidwe 25:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 196

Machitidwe 25:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yoh 19:13; Mac 12:21; 25:17

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 197-198

Machitidwe 25:7

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 5:11; Lu 23:2; Mac 24:5

Machitidwe 25:8

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 24:12
  • +Mac 28:17

Machitidwe 25:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 24:27
  • +Mac 25:20

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 197-198

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2001, ptsa. 23-24

Machitidwe 25:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:21; 26:32
  • +Mac 28:17

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 198

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2001, ptsa. 23-24

Machitidwe 25:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Pe 4:15
  • +Mac 23:29; 26:31
  • +Mac 25:21; 26:32; 28:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 198

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    9/2016, ptsa. 15-16

    Nsanja ya Olonda,

    7/1/2011, tsa. 29

    5/15/2008, tsa. 32

    12/15/2001, ptsa. 23-24

    6/15/1997, ptsa. 30-31

    11/1/1990, ptsa. 10-11

    6/15/1990, tsa. 24

Machitidwe 25:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 198

    Nsanja ya Olonda,

    3/1/2015, tsa. 12

Machitidwe 25:13

Mawu a M'munsi

  • *

    Ameneyu anali Herode Agiripa Wachiwiri.

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 198, 201

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 24

Machitidwe 25:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:2

Machitidwe 25:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    12/15/2001, tsa. 23

Machitidwe 25:18

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:7

Machitidwe 25:19

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 18:15; 23:29
  • +Mac 22:8

Machitidwe 25:20

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:9

Machitidwe 25:21

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:11; 26:32; 28:19

Machitidwe 25:22

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 9:15

Machitidwe 25:23

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Pe 1:24; 1Yo 2:16

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    9/1/1998, tsa. 30

Machitidwe 25:24

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 22:22

Machitidwe 25:25

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 23:29; 26:31
  • +Mac 25:21

Machitidwe 25:26

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 26:32

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

Mac. 25:1Mac 24:27
Mac. 25:1Mac 21:15
Mac. 25:2Mac 24:1; 25:15
Mac. 25:3Sl 37:32; Miy 1:16; Mac 9:23; 14:5; 23:21; 2Ak 11:26
Mac. 25:5Mac 25:16
Mac. 25:6Yoh 19:13; Mac 12:21; 25:17
Mac. 25:7Mt 5:11; Lu 23:2; Mac 24:5
Mac. 25:8Mac 24:12
Mac. 25:8Mac 28:17
Mac. 25:9Mac 24:27
Mac. 25:9Mac 25:20
Mac. 25:10Mac 25:21; 26:32
Mac. 25:10Mac 28:17
Mac. 25:111Pe 4:15
Mac. 25:11Mac 23:29; 26:31
Mac. 25:11Mac 25:21; 26:32; 28:19
Mac. 25:15Mac 25:2
Mac. 25:16Mac 25:5
Mac. 25:18Mac 25:7
Mac. 25:19Mac 18:15; 23:29
Mac. 25:19Mac 22:8
Mac. 25:20Mac 25:9
Mac. 25:21Mac 25:11; 26:32; 28:19
Mac. 25:22Mac 9:15
Mac. 25:231Pe 1:24; 1Yo 2:16
Mac. 25:24Mac 22:22
Mac. 25:25Mac 23:29; 26:31
Mac. 25:25Mac 25:21
Mac. 25:26Mac 26:32
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano (nwt)
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Machitidwe 25:1-27

Machitidwe

25 Patatha masiku atatu Fesito atayamba kulamulira+ m’chigawocho, anapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kaisareya.+ 2 Kumeneko ansembe aakulu ndi amuna olemekezeka pakati pa Ayuda anamuuza zambiri+ zoneneza Paulo. Ndiyeno anayamba kumuchonderera, 3 ndi kumupempha kuti awakomere mtima mwa kuitanitsa munthuyu kuti abwere ku Yerusalemu, kuti iwo amudikirire+ panjira ndi kumupha. 4 Koma Fesito anawayankha kuti Paulo akuyenera kusungidwa ku Kaisareya, ndi kuti posachedwa nayenso anyamuka kupita komweko. 5 Ndiyeno anati: “Amene ali ndi maudindo pakati panu, tipitire limodzi kuti ngati pali cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu akamuimbe mlandu.”+

6 Choncho iye atakhala nawo kumeneko kwa masiku osapitirira 8 kapena 10, anapita ku Kaisareya. Ndipo tsiku lotsatira anakhala pampando woweruzira milandu+ ndi kuitanitsa Paulo kuti abwere naye. 7 Paulo atafika, Ayuda amene anabwera kuchokera ku Yerusalemu, anaima momuzungulira n’kumamuneneza milandu yoopsa yambiri,+ imene sanathe kupereka umboni wake.

8 Koma Paulo podziteteza anati: “Ine sindinachimwire Chilamulo cha Ayuda, kapena kachisi,+ kapena Kaisara.”+ 9 Koma pofuna kuti Ayudawo amukonde,+ Fesito anayankha Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhani imeneyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?”+ 10 Paulo anayankha kuti: “Ine ndaimirira kutsogolo kwa mpando woweruzira milandu wa Kaisara,+ kumene ndiyenera kuweruzidwa. Ayuda+ sindinawalakwire chilichonse, monga mmene inunso mukuonera. 11 Ngati ndilidi wolakwa,+ ndipo ndachita chinthu choyenera imfa, sindikukana kufa.+ Koma ngati pa zimene awa akundinenezazi palibe chinthu chotero, palibe munthu amene angandipereke kwa iwo kuti awakondweretse. Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!”+ 12 Ndiyeno Fesito atalankhula ndi bungwe la aphungu, anayankha kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekera kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.”

13 Tsopano patapita masiku angapo, Mfumu Agiripa* ndi Berenike anafika ku Kaisareya pa ulendo wa boma wokapereka ulemu kwa Fesito. 14 Pamene anali kumeneko masiku angapo, Fesito anafotokozera mfumuyo nkhani yokhudza Paulo. Iye ananena kuti:

“Pali munthu wina amene Felike anamusiya m’ndende, 15 ndipo pamene ndinali ku Yerusalemu, ansembe aakulu komanso akulu a Ayuda anabwera kudzamuneneza.+ Anali kupempha kuti apatsidwe chiweruzo chakuti aphedwe. 16 Koma ine ndinawayankha kuti, Aroma sachita zinthu mwa njira imeneyo. Iwo sapereka munthu m’manja mwa omuneneza pongofuna kuwakondweretsa, munthu wonenezedwayo+ asanapatsidwe mwayi woonana pamasom’pamaso ndi omunenezawo kuti alankhule mawu odziteteza pa mlanduwo. 17 Choncho onse atafika kuno, sindinachedwe, koma tsiku lotsatira ndinakhala pampando woweruzira milandu ndi kuitanitsa munthuyo kuti abwere naye. 18 Omunenezawo ataimirira, sanatchule mlandu uliwonse+ wa zoipa zimene ndinali kuganiza zokhudza munthu ameneyu. 19 Iwo anali kungotsutsana naye nkhani zokhudzana ndi kulambira+ kwawo mulungu, ndi za munthu wina wake wotchedwa Yesu amene anafa koma Paulo akupitiriza kunena motsimikiza kuti ali moyo.+ 20 Choncho pothedwa nzeru ndi mkangano wa nkhani zimenezi, ndinamufunsa ngati akufuna kupita ku Yerusalemu kuti nkhanizi zikaweruzidwire kumeneko.+ 21 Koma pamene Paulo anapempha+ kuti timusunge kuti akamve chigamulo cha Wolemekezeka, ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”

22 Pamenepo Agiripa anauza Fesito kuti: “Inenso ndikufuna ndimve ndekha munthu ameneyu+ akulankhula.” Iye anati: “Mawa mudzamumvetsera.” 23 M’mawa wake, Agiripa ndi Berenike anabwera ndi ulemu waukulu wachifumu.+ Analowa m’chipinda chosonkhanira pamodzi ndi akuluakulu a asilikali komanso akuluakulu a mumzindawo, ndipo Fesito atalamula, anamubweretsa Paulo. 24 Ndiyeno Fesito ananena kuti: “Mfumu Agiripa ndi anthu nonse amene muli nafe pano, mukumuona munthu uyu. Ayuda onse anandipempha ine ku Yerusalemu komanso kuno, mofuula kuti iyeyu sayeneranso kukhala ndi moyo.+ 25 Koma ine ndinaona kuti sanachite chilichonse choyenera imfa.+ Choncho iyeyu atapempha kuti akaonekere kwa Wolemekezeka,+ ndinaganiza zomutumiza. 26 Koma ndilibe chenicheni chimene ndingalembere Mbuyanga chokhudza munthuyu. Choncho ndamubweretsa pamaso panu, makamaka pamaso pa inu, Mfumu Agiripa, kuti mukamufunsa za nkhaniyi,+ ndipeze cholemba. 27 Chifukwa kwa ine, ndikuona kuti si chanzeru kutumiza mkaidi koma osanena milandu imene akumuneneza.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena