Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 27
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Machitidwe 27:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 25:12

Machitidwe 27:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 19:29; 20:4; Akl 4:10

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 204

    Nsanja ya Olonda,

    9/15/1997, ptsa. 30-31

Machitidwe 27:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Miy 19:22; Mac 28:16
  • +Mac 24:23

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 204

Machitidwe 27:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 204-205, 208

Machitidwe 27:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 204-205, 208

Machitidwe 27:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 28:11

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 205, 208

    Nsanja ya Olonda,

    3/15/1999, ptsa. 29-30

Machitidwe 27:7

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 205

Machitidwe 27:8

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 205-207

Machitidwe 27:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Le 16:29; 23:27

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 205-207

    Nsanja ya Olonda (Yogawira),

    No. 5 2017, tsa. 9

    Nsanja ya Olonda,

    2/1/2010, tsa. 23

    3/15/1999, tsa. 31

Machitidwe 27:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 27:21

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yogawira),

    No. 5 2017, tsa. 9

    Nsanja ya Olonda,

    3/15/1999, tsa. 31

Machitidwe 27:11

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 207

Machitidwe 27:12

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 207

    Nsanja ya Olonda,

    3/15/1999, tsa. 31

Machitidwe 27:14

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mko 4:37

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 207

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 24

Machitidwe 27:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 27:32

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 207

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/1990, tsa. 26

Machitidwe 27:17

Mawu a M'munsi

  • *

    “Suriti” ndi malo awiri akuluakulu osazama a m’nyanja. Malo amenewa ali ku Libiya kumpoto kwa Afirika ndipo pamapezeka milu yambiri ya mchenga.

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 207

    Galamukani!,

    10/8/1996, tsa. 15

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 24

    5/15/1990, tsa. 26

Machitidwe 27:18

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yon 1:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 24

Machitidwe 27:19

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 207

    Nsanja ya Olonda,

    6/15/1990, tsa. 24

Machitidwe 27:20

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yon 1:13

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 207

Machitidwe 27:21

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yon 1:9
  • +Mac 27:10

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 207-208

Machitidwe 27:22

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 207-208

Machitidwe 27:23

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Da 6:16; Mac 5:19; 23:11; Ahe 1:14
  • +Aro 1:9; 2Ti 1:3; Ahe 12:28

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 208

Machitidwe 27:24

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 23:11; 25:11

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda (Yophunzira),

    9/2016, ptsa. 15-16

Machitidwe 27:25

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Nu 23:19; Aro 4:21; Tit 1:2

Machitidwe 27:26

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 28:1

Machitidwe 27:27

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 209

    Nsanja ya Olonda,

    6/1/1993, ptsa. 3-4

Machitidwe 27:29

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 209

Machitidwe 27:30

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    5/1/1999, tsa. 30

Machitidwe 27:31

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 27:22

Machitidwe 27:32

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 27:16

Machitidwe 27:34

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Sa 14:45; 2Sa 14:11; Mt 10:30; Lu 12:7

Machitidwe 27:35

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 15:36; Mko 8:6; Yoh 6:11; Aro 14:6; 1Ti 4:4

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, ptsa. 206, 209

Machitidwe 27:38

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yon 1:5

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 209

Machitidwe 27:39

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 28:1

Machitidwe 27:40

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 209

Machitidwe 27:41

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 27:22; 2Ak 11:25

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Kuchitira Umboni Mokwanira, tsa. 209

Machitidwe 27:42

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    5/1/1999, tsa. 30

Machitidwe 27:44

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 27:24

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

Mac. 27:1Mac 25:12
Mac. 27:2Mac 19:29; 20:4; Akl 4:10
Mac. 27:3Miy 19:22; Mac 28:16
Mac. 27:3Mac 24:23
Mac. 27:6Mac 28:11
Mac. 27:9Le 16:29; 23:27
Mac. 27:10Mac 27:21
Mac. 27:14Mko 4:37
Mac. 27:16Mac 27:32
Mac. 27:18Yon 1:5
Mac. 27:20Yon 1:13
Mac. 27:21Yon 1:9
Mac. 27:21Mac 27:10
Mac. 27:23Da 6:16; Mac 5:19; 23:11; Ahe 1:14
Mac. 27:23Aro 1:9; 2Ti 1:3; Ahe 12:28
Mac. 27:24Mac 23:11; 25:11
Mac. 27:25Nu 23:19; Aro 4:21; Tit 1:2
Mac. 27:26Mac 28:1
Mac. 27:31Mac 27:22
Mac. 27:32Mac 27:16
Mac. 27:341Sa 14:45; 2Sa 14:11; Mt 10:30; Lu 12:7
Mac. 27:35Mt 15:36; Mko 8:6; Yoh 6:11; Aro 14:6; 1Ti 4:4
Mac. 27:38Yon 1:5
Mac. 27:39Mac 28:1
Mac. 27:41Mac 27:22; 2Ak 11:25
Mac. 27:44Mac 27:24
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano (nwt)
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
  • 28
  • 29
  • 30
  • 31
  • 32
  • 33
  • 34
  • 35
  • 36
  • 37
  • 38
  • 39
  • 40
  • 41
  • 42
  • 43
  • 44
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Machitidwe 27:1-44

Machitidwe

27 Tsopano ulendo wathu wa pamadzi wopita ku Italiya utatsimikizika,+ anapereka Paulo ndi akaidi ena m’manja mwa kapitawo wa asilikali dzina lake Yuliyo, wa m’gulu la asilikali la Augusito. 2 Ku Adiramutiyo tinakwera ngalawa imene inali pafupi kunyamuka ulendo wopita kumalo osiyanasiyana a m’mphepete mwa nyanja m’chigawo cha Asia. Kenako tinanyamuka, tilinso limodzi ndi Arisitako,+ yemwe anali Mmakedoniya wa ku Tesalonika. 3 Tsiku lotsatira tinafika ku Sidoni, ndipo Yuliyo anakomera mtima kwambiri+ Paulo ndipo anamulola kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalire.+

4 Titalowanso panyanja kuchokera kumeneko, tinayenda m’mphepete mwa chilumba cha Kupuro chimene chinatitchinjiriza ku mphepo imene inali kuwomba kuchokera kumene ife tinali kupita. 5 Tinayenda pakati pa nyanja molambalala Kilikiya ndi Pamfuliya, ndipo tinafika ku Mura, ku Lukiya. 6 Kumeneko kapitawo wa asilikali anapeza ngalawa yochokera ku Alekizandiriya+ imene inali kupita ku Italiya, ndipo anatikweza mmenemo. 7 Choncho tinayenda pang’onopang’ono kwa masiku ambiri ndipo tinafika ku Kinido movutikira. Polephera kupitirira chifukwa cha mphepo, tinadzera ku Salimone kuti chilumba cha Kerete chititchinge ku mphepo. 8 Titayenda movutikira m’mbali mwa chilumba chimenechi, tinafika pamalo ena otchedwa Madoko Okoma, amene anali pafupi ndi mzinda wa Laseya.

9 Popeza panali patapita kale nthawi yaitali, ndipo kuyenda panyanja tsopano kunali koopsa chifukwa ngakhale nthawi ya kusala kudya kwa tsiku la mwambo wophimba machimo+ inali itadutsa kale, Paulo anawapatsa malangizo. 10 Iye anawauza kuti: “Amuna inu, ndikuona kuti ulendowu tikauyamba panopa tiwonongetsa zambiri. Tiwonongetsa katundu ndi ngalawa, ngakhalenso miyoyo yathu.”+ 11 Koma kapitawo wa asilikaliyo anamvera woyendetsa ngalawa ndi mwiniwake wa ngalawayo m’malo momvera zimene Paulo ananena. 12 Popeza dokolo silinali labwino kukhalapo nyengo yachisanu, anthu ambiri analimbikitsa zakuti achoke pamalopo. Iwo ankafuna kuona ngati n’zotheka kukafika ku Finikesi kuti akakhale kumeneko nyengo yachisanu. Finikesi linali doko la Kerete loloza kumpoto chakum’mawa ndi kum’mwera chakum’mawa.

13 Ndiponso, mphepo ya kum’mwera itayamba kuwomba pang’onopang’ono, anaganiza kuti tsopano zimene anali kufuna zitheka. Choncho anakoka nangula n’kuyamba kuyenda m’mphepete mwa chilumba cha Kerete. 14 Koma posakhalitsa, mphepo yamkuntho+ yotchedwa Yulakilo inawomba ngalawayo. 15 Popeza ngalawa inali kuwombedwa ndi mphepo yamphamvu, ndipo sitinathe kuiwongolera kuti iyende moyang’anana ndi mphepoyo, tinagonja ndi kutengedwa nayo. 16 Tsopano tinayenda m’mphepete mwa chilumba china chaching’ono chotchedwa Kauda chimene chinali kutitchinjiriza ku mphepo. Komabe tinali kulephera kuwongolera bwato laling’ono limene ngalawayo inali kukoka.+ 17 Ndiyeno atakweza bwatolo m’ngalawa, anayamba kukulunga ngalawayo ndi zomangira kuti ilimbe. Ndipo poopa kuti ngalawa ingatitimire mumchenga pa Suriti,* iwo anatsitsa zingwe zomangira chinsalu cha ngalawa moti anali kukankhidwa ndi mphepo. 18 Koma popeza kuti mphepo yamkuntho inali kutiwomba ndi kutikankha mwamphamvu, tsiku lotsatira anthu anayamba kutaya katundu kuti ngalawa ipepukidwe.+ 19 Tsiku lachitatu, anataya ndi manja awo zingwe zokwezera chinsalu cha ngalawayo.

20 Tsopano poona kuti dzuwa kapena nyenyezi sizinaoneke kwa masiku ambiri, ndipo tinali kukankhidwa ndi chimphepo champhamvu,+ chiyembekezo choti tipulumuka chinatheratu. 21 Ndipo atakhala nthawi yaitali osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pawo+ ndi kunena kuti: “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga, osachoka ku Kerete kuja, ndithu zinthu sizikanawonongeka ndi kutayika chonchi.+ 22 Komabe, ndikukuuzani kuti mukhale osangalala, chifukwa palibe aliyense wa inu amene ataye moyo wake, koma ngalawa yokhayi iwonongeka. 23 Pakuti usiku mngelo+ wa Mulungu wanga, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika, anaima pafupi nane,+ 24 ndi kunena kuti, ‘Usaope Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara,+ ndipo taona! Chifukwa cha iwe, Mulungu mokoma mtima adzapulumutsa onse amene uli nawo pa ulendowu.’ 25 Choncho khalani osangalala amuna inu, pakuti ndikukhulupirira Mulungu+ kuti zonse zichitika ndendende mmene wandiuzira. 26 Komabe, ngalawa yathuyi iwonongeka pafupi ndi chilumba chinachake.”+

27 Tsopano usiku wa 14 unafika ndipo mphepo inali kutikankhira uku ndi uku panyanja ya Adiriya. Ndiyeno pakati pa usiku, ogwira ntchito mungalawa anayamba kuganiza kuti akuyandikira kumtunda. 28 Choncho anayeza kuzama kwa nyanja ndi kupeza kuti inali mamita 36. Atayenda kamtunda pang’ono anayezanso kuzama kwa nyanja ndi kupeza mamita 27. 29 Koma poopa kuti tikawomba miyala, anatsitsa anangula anayi kumbuyo kwa ngalawayo, ndipo anali kulakalaka kutangocha. 30 Tsopano ogwira ntchito m’ngalawamo anafuna kuthawamo. Anatsitsira bwato lija panyanja ponamizira kuti akufuna kutsitsa anangula kutsogolo kwa ngalawayo. 31 Koma Paulo anauza kapitawo wa asilikali ndi asilikaliwo kuti: “Anthu awa akapanda kukhalabe m’ngalawa muno, simupulumuka.”+ 32 Pamenepo asilikali anadula zingwe za bwatolo+ n’kulisiya kuti lipite.

33 Kutatsala pang’ono kucha, Paulo anayamba kulimbikitsa onse kuti adye chakudya. Iye anati: “Lero mwakwanitsa masiku 14 mukuchezera ndi kusala kudya, chifukwa mukungokhala osadya chilichonse. 34 Choncho ndikukulimbikitsani kuti mudye kuti zinthu zikuyendereni bwino. Pakuti ngakhale tsitsi+ limodzi la kumutu kwa aliyense wa inu siliwonongeka.” 35 Atanena zimenezi, anatenga mkate. Kenako anayamika+ kwa Mulungu pamaso pa onse n’kunyema mkatewo ndi kuyamba kudya. 36 Pamenepo onse anasangalala ndipo anayamba kudya chakudya. 37 Tonse pamodzi, m’ngalawamo tinalimo anthu 276. 38 Onse atadya ndi kukhuta, anayamba kutayira tirigu m’nyanja kuti ngalawa ija ipepukidwe.+

39 Potsirizira pake kutacha, sanathe kuzindikira dzikolo, koma anali kuona gombe linalake la mchenga, ndipo anafunitsitsa kuti ngati n’kotheka akaimitse+ ngalawa pamenepo. 40 Choncho anadula anangula ndi kuwagwetsera m’nyanja. Anamasulanso zingwe zomangira nkhafi zowongolera. Atakweza m’mwamba nsalu ya kutsogolo ya ngalawa, analunjika kugombelo. 41 Pamene anafika pachimulu cha mchenga m’madzimo, chimene mafunde anali kuchiwomba mbali zonse, ngalawa yawo inatitimira mumchengamo. Kutsogolo kwa ngalawayo kunakanirira pansi osasunthika, ndipo mafunde amphamvu anayamba kuwomba kumbuyo kwake moti inayamba kusweka zidutswazidutswa.+ 42 Zitatero asilikali anaganiza zopha akaidi, kuti pasapezeke aliyense wosambira n’kuthawa. 43 Koma kapitawo wa asilikali anafunitsitsa kuti Paulo akafike naye ali bwinobwino, choncho anawaletsa kuchita zimene amafunazo. Ndiyeno analamula odziwa kusambira kuti alumphire m’nyanjamo kuti akhale oyamba kukafika kumtunda. 44 Analamulanso ena onse kuti achite chimodzimodzi, ena pamatabwa ndipo ena pa zinthu zina zochokera kungalawayo. Ndipo pamapeto pake onse anafika kumtunda ali bwinobwino.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena