Yeremiya
23 “Tsoka abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pamalo anga odyetsera ziweto!”+ watero Yehova.
2 Yehova Mulungu wa Isiraeli wadzudzula abusa amene akuweta anthu ake kuti: “Inu mwabalalitsa nkhosa zanga. Mukupitiriza kuzimwaza ndipo simukuzisamalira.”+
“Tsopano ndikutembenukira kwa inu chifukwa cha zochita zanu zoipazo,”+ watero Yehova.
3 “Ine ndidzasonkhanitsa pamodzi nkhosa zanga zotsala kuchokera m’mayiko onse kumene ndinazibalalitsira+ ndipo ndidzazibwezeretsa kumalo awo kumene zimadyera.+ Nkhosazo zidzaberekana ndi kuchuluka.+ 4 Ndidzapatsa nkhosazo abusa ndipo adzaziweta.+ Sizidzaopanso kanthu kapena kugwidwa ndi mantha aakulu,+ ndipo palibe imene idzasowa,” watero Yehova.
5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ 6 M’masiku a mfumu imeneyi, Yuda adzapulumutsidwa,+ ndipo Isiraeli adzakhala mwabata.+ Dzina la mfumuyi lidzakhala Yehova Ndiye Chilungamo Chathu.”+
7 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene sadzalumbiranso kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo.’+ 8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+
9 Mtima wanga wasweka mkati mwanga chifukwa cha aneneri. Mafupa anga onse ayamba kunjenjemera. Ndakhala ngati munthu woledzera,+ komanso mwamuna wamphamvu amene wagonjetsedwa ndi vinyo, chifukwa cha Yehova komanso chifukwa cha mawu ake oyera. 10 Dzikoli ladzaza+ ndi anthu achigololo+ ndipo chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+ ndipo malo a m’chipululu odyetsera ziweto auma.+ Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo mopanda chilungamo.
11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa+ ndipo m’nyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ watero Yehova. 12 “Choncho, njira zawo zidzawakhalira ngati malo oterera+ amdima ndipo adzawakankhira m’njirazo moti adzagwa.”+
“Pakuti ndidzawagwetsera tsoka, tsiku la chilango chawo lidzafika,”+ watero Yehova. 13 “Ndaona zosayenera mwa aneneri a ku Samariya.+ Iwo atumikira ngati aneneri a Baala+ ndipo asocheretsa anthu anga, Aisiraeli.+ 14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa.+ Iwo achita chigololo+ ndi kuchita zinthu mwachinyengo.+ Alimbikitsa anthu ochita zoipa kuti aliyense asafooke ndi kusiya+ kuchita zoipa zake. Kwa ine, onsewo akhala ngati Sodomu+ ndipo anthu okhala mumzindawu akhala ngati Gomora.”+
15 Choncho Yehova wa makamu wadzudzula aneneriwo kuti: “Ndiwadyetsa chitsamba chowawa ndipo ndiwamwetsa madzi apoizoni.+ Chifukwa kuchokera mwa aneneri a ku Yerusalemu mpatuko+ wafalikira m’dziko lonse.”
16 Yehova wa makamu wanena kuti: “Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa anthu inu.+ Akukulimbikitsani kuchita zinthu zopanda pake.+ Iwo akulankhula masomphenya a mumtima mwawo+ osati ochokera m’kamwa mwa Yehova.+ 17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+ 18 Ndani waimirira pagulu la anthu amene Yehova amawakonda+ kuti azindikire ndi kumva mawu ake?+ Ndani watchera khutu kuti amvetsere mawu ake?+ 19 Taonani! Mphepo yamkuntho yochokera kwa Yehova idzawomba. Mkwiyo wake udzawomba ngati kamvulumvulu wamphamvu.+ Udzawomba pamitu ya anthu oipawo.+ 20 Mkwiyo wa Yehova sudzatha kufikira atachita zofuna za mtima wake+ ndi kuzikwaniritsa.+ M’masiku otsiriza, anthu inu mudzalingalira zimenezi ndipo mudzazimvetsa.+
21 “Ine sindinatumize aneneriwo, koma okha anathamanga. Ine sindinalankhule nawo, koma okha analosera.+ 22 Ngati iwo akanaima pagulu la anthu amene ndimawakonda,+ akanachititsa anthu anga kumva mawu anga, ndipo akanabweza anthu anga panjira zawo zoipa komanso pa zochita zawo zoipa.”+
23 Yehova wanena kuti: “Kodi ine ndine Mulungu amene amangokhala pafupi, osati Mulungu amenenso ali kutali?”+
24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova.
“Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova. 25 “Ndamva zimene aneneri akulosera monama m’dzina langa+ kuti, ‘Ndalota maloto! Ndalota maloto!’+ 26 Kodi aneneri amene akulosera monamawa, amene akunenera chinyengo cha mumtima mwawo, adzakhala ndi chinyengo chimenechi mumtima mwawo kufikira liti?+ 27 Iwo akuganiza zochititsa anthu anga kuiwala dzina langa pogwiritsa ntchito maloto amene aneneriwo amauzana nthawi zonse,+ monga mmene makolo awo anaiwalira dzina langa chifukwa cha Baala.+ 28 Mneneri amene walota maloto anene maloto akewo. Koma amene ndamuuza mawu anga, alankhule mawu angawo moona.”+
“Kodi mapesi a tirigu angafanane ndi tirigu weniweniyo?”+ watero Yehova.
29 Yehova wanena kuti: “Kodi mawu anga safanana ndi moto?+ Kodi safanana ndi nyundo imene imaphwanya thanthwe?”+
30 “Chotero ndikutsutsana ndi aneneriwo+ chifukwa aliyense wa iwo akuba mawu anga kwa mnzake,”+ watero Yehova.
31 Yehova wanena kuti: “Ine ndikutsutsana ndi aneneriwo chifukwa akugwiritsa ntchito lilime lawo ndi kunena kuti, ‘Awa ndi mawu ochokera kwa Mulungu!’”+
32 “Ine ndikutsutsana ndi aneneri amene akulota maloto onama, amene akunena malotowo ndi kusocheretsa anthu anga ndi bodza lawo+ komanso ndi kudzitama kwawo,”+ watero Yehova.
“Koma ine sindinawatume kapena kuwalamula kuchita zimenezo. Choncho sadzachita zopindulitsa anthu awa,”+ watero Yehova.
33 “Anthu awa, aneneri, kapena ansembe akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga* wa Yehova ukuti chiyani?’+ uwayankhe kuti, ‘“Anthu inu ndinu katundu wolemetsa!+ Ndipo ndidzakusiyani,”+ watero Yehova.’ 34 Mneneri, wansembe, kapena aliyense amene akunena kuti, ‘Uthenga uwu ndi katundu wolemetsa wa Yehova!’ ndidzatembenukira kwa iye ndi kwa nyumba yake.+ 35 Aliyense wa inu akuuza mnzake ndi m’bale wake kuti, ‘Kodi Yehova wayankha kuti chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?’+ 36 Koma anthu inu musanenenso kuti uthenga wa Yehova ndi katundu wolemetsa,+ pakuti mawu a aliyense wa inu ndi katundu wake wolemetsa,+ pakuti mwasintha mawu a Mulungu wathu wamoyo,+ Yehova wa makamu.
37 “Mneneri umufunse kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?+ 38 Ndipo mukapitiriza kunena kuti, “Uthenga uwu ndi katundu wolemetsa wa Yehova!” Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti mukunenabe kuti, ‘Mawu a Yehova ndi katundu wolemetsa,’ pamene ine ndinakuuzani kuti ‘Musamanene kuti: “Mawu a Yehova ndi katundu wolemetsa!”’ 39 tsopano ine ndikukusiyani nokhanokha anthu inu.+ Ndikusiya inuyo ndi mzinda umene ndinapatsa inu ndi makolo anu. Ndikuchita zimenezi kuti musakhalenso pamaso panga.+ 40 Ndidzaika chitonzo pa inu mpaka kalekale ndipo mudzanyozeka mpaka kalekale. Zimenezi sizidzaiwalika.”’”+