Yesaya
1 Masomphenya+ amene Yesaya+ mwana wa Amozi anaona, okhudza Yuda ndi Yerusalemu m’masiku a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda:+
2 Imvani+ kumwamba inu, ndipo tchera khutu iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena kuti: “Ndalera ana ndi kuwakulitsa,+ koma iwo andipandukira.+ 3 Ng’ombe yamphongo imam’dziwa bwino munthu amene anaigula, ndipo bulu amadziwa chinthu chimene mbuye wake amam’dyetseramo. Koma Isiraeli sandidziwa,+ ndipo anthu anga sanachite zinthu mozindikira.”+
4 Tsoka kwa mtundu wochimwa,+ anthu olemedwa ndi zolakwa, mbewu yochita zoipa,+ ana obweretsa chiwonongeko.+ Iwo amusiya Yehova.+ Achitira Woyera wa Isiraeli zinthu zopanda ulemu,+ ndipo abwerera m’mbuyo.+ 5 Kodi mumenyedwanso pati+ mmene mukupitiriza kupandukamu?+ Mutu wanu uli ndi zilonda zokhazokha, ndipo mtima wanu wafooka.+ 6 Kuyambira kuphazi mpaka kumutu palibe pabwino.+ Thupi lanu lonse lili ndi mabala ndi zilonda, ndiponso lanyukanyuka. Palibe amene wafinya zilonda zanuzo kapena kuzimanga. Palibenso amene wazifewetsa ndi mafuta.+ 7 Dziko lanu lawonongedwa.+ Mizinda yanu yatenthedwa ndi moto,+ ndipo alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona.+ Chilichonse chawonongeka ngati mmene zimakhalira adani akalanda dziko.+ 8 Mwana wamkazi wa Ziyoni+ wasiyidwa ngati msasa m’munda wa mpesa, ngati chisimba* m’munda wa minkhaka, ndiponso ngati mzinda umene wazunguliridwa ndi adani.+ 9 Yehova wa makamu akanapanda kutisiyira anthu ochepa opulumuka,+ tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.+
10 Imvani mawu a Yehova,+ inu olamulira ankhanza+ a ku Sodomu.+ Mvetserani malamulo a Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora. 11 Yehova wanena kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine? Nsembe zopsereza zathunthu+ za nkhosa zamphongo+ ndiponso mafuta a nyama zodyetsedwa bwino zandikwana.+ Ine sindikusangalalanso+ ndi magazi+ a ana a ng’ombe amphongo, ana a nkhosa amphongo ndiponso a mbuzi zamphongo.+ 12 Inu mukamabwerabwera kuti mudzaone nkhope yanga,+ kodi ndani wakuuzani kuti muchite zimenezi, kuti muzipondaponda mabwalo a panyumba panga?+ 13 Musabweretsenso nsembe zina zaufa zopanda phindu.+ Zofukiza zanu ndikunyansidwa nazo.+ Mumasunga masiku okhala mwezi+ ndi sabata,+ ndipo mumaitanitsa misonkhano.+ Koma ine ndatopa kukuonani mukugwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga+ pamene mukuchita misonkhano yapadera. 14 Moyo wanga ukudana ndi masiku anu okhala mwezi ndi zikondwerero zanu.+ Zimenezi zasanduka katundu wolemera kwa ine,+ ndipo ndatopa kuzinyamula.+ 15 Mukatambasula manja anu,+ ndimakubisirani maso anga.+ Ngakhale mupereke mapemphero ambiri,+ ine sindimvetsera.+ Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.+ 16 Sambani,+ dziyeretseni.+ Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga.+ Lekani kuchita zoipa.+ 17 Phunzirani kuchita zabwino.+ Funafunani chilungamo.+ Dzudzulani munthu wopondereza ena.+ Weruzani mwachilungamo mwana wamasiye.*+ Thandizani mkazi wamasiye pa mlandu wake.”+
18 Yehova akuti, “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+ Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.+ Ngakhale atakhala ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje. 19 Mukakhala ndi mtima wofuna kundimvera, mudzadya zabwino za m’dziko lanu.+ 20 Koma mukakana+ n’kupanduka, mudzawonongedwa ndi lupanga, chifukwa pakamwa pa Yehova m’pamene panena zimenezi.”+
21 Taonani! Mzinda wokhulupirika uja+ wasanduka hule.+ Unali wodzaza ndi chilungamo+ ndipo zachilungamo zinali kukhala mwa iye,+ koma tsopano muli zigawenga zopha anthu.+ 22 Siliva wako wasanduka zonyansa.*+ Mowa wako wa tirigu wasukuluka ndi madzi.+ 23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+
24 Choncho mawu a Ambuye woona, Yehova wa makamu, Wamphamvu wa Isiraeli,+ ndi akuti: “Eya! Ndidzibweretsera mpumulo pochotsa adani anga ndipo ndibwezera+ odana nane.+ 25 Ndidzakutembenuzirani dzanja langa. Ndidzasungunula zonyansa zanu zonse, ndipo ndidzachotsa nyansi zanu zonse.+ 26 Ndidzakubweretseraninso oweruza ngati pa chiyambi paja, ndi aphungu ngati poyamba paja.+ Pambuyo pa zimenezi mudzatchedwa Mzinda Wachilungamo ndi Mzinda Wokhulupirika.+ 27 Ziyoni adzapulumutsidwa+ ndi chilungamo ndipo anthu ake amene adzabwerere, adzapulumutsidwanso ndi chilungamo.+ 28 Kuwonongeka kwa opanduka ndi kwa ochimwa kudzachitikira limodzi,+ ndipo anthu omusiya Yehova adzatha.+ 29 Pakuti anthu adzachita manyazi ndi mitengo ikuluikulu imene inu munali kuilakalaka,+ ndipo mudzagwetsa nkhope zanu chifukwa cha minda imene mwasankha.+ 30 Pakuti mudzakhala ngati mtengo waukulu umene masamba ake akufota+ ndiponso ngati munda umene ulibe madzi. 31 Munthu wamphamvu adzakhala ngati chingwe chabwazi,+ ndipo ntchito yake idzakhala ngati kamoto kakang’ono. Zonsezi zidzayakira limodzi popanda wozizimitsa.”+