Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Mark 1:1-16:20
  • Maliko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maliko
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Maliko

Maliko

1 Chiyambi cha uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu: 2 Monga mmene analembera m’buku la mneneri Yesaya kuti: “(Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga pamaso pako, amene adzakonza njira yako.)*+ 3 Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti, ‘Konzani njira ya Yehova* anthu inu, wongolani misewu yake,’”+ 4 Yohane m’batizi anafika m’chipululu, ndipo anali kulalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ 5 Choncho onse okhala m’dera la Yudeya ndi onse okhala mu Yerusalemu anakhamukira kwa iye. Chotero iye anawabatiza mumtsinje wa Yorodano ndipo anthuwo anali kuulula machimo awo poyera.+ 6 Yohane ameneyu anali kuvala chovala cha ubweya wa ngamila ndi lamba wachikopa m’chiuno mwake,+ ndipo anali kudya dzombe+ ndi uchi.+ 7 Iye anali kulalikira kuti: “Pambuyo pangapa pakubwera winawake wamphamvu kuposa ine; ine sindili woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake.+ 8 Ine ndakubatizani ndi madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.”+

9 M’masiku amenewo, Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu Yorodano.+ 10 Atangovuuka m’madzimo, iye anaona kumwamba kukutseguka, ndiponso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera.+ 11 Pamenepo panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”+

12 Nthawi yomweyo mzimuwo unamulimbikitsa kupita kuchipululu.+ 13 Chotero iye anakhala m’chipululumo masiku 40,+ akuyesedwa ndi Satana.+ M’chipululumo munalinso nyama zakutchire. Pambuyo pake, angelo anam’tumikira.+

14 Tsopano Yohane ataponyedwa m’ndende, Yesu anapita ku Galileya+ kukalalikira uthenga wabwino wa Mulungu+ 15 kuti: “Nthawi yoikidwiratu yakwaniritsidwa!+ Ufumu wa Mulungu wayandikira! Lapani+ anthu inu! Khulupirirani uthenga wabwino!”

16 Pamene anali kuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya* Yesu anaona Simoni+ ndi Andireya m’bale wake wa Simoni, akuponya maukonde awo m’nyanjamo, pakuti anali asodzi.+ 17 Chotero Yesu anawauza kuti: “Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 18 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatira.+ 19 Atapita patsogolo pang’ono, anaona Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi m’bale wake Yohane, ali mu ngalawa yawo akusoka maukonde awo.+ 20 Nthawi yomweyo anawaitana. Iwonso anasiya bambo wawo Zebedayo m’ngalawamo limodzi ndi anthu aganyu, ndipo anam’tsatira. 21 Onsewo anachoka ndi kupita ku Kaperenao.+

Litangofika tsiku la sabata anakalowa m’sunagoge ndi kuyamba kuphunzitsa. 22 Mmenemo anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro, osati monga alembi.+ 23 Komanso pa nthawi yomweyo, m’sunagoge mwawomo munali munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa, ndipo munthuyo anafuula,+ 24 kuti: “Kodi tili nanu chiyani, Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani+ bwino kwambiri, ndinu Woyera+ wa Mulungu.”+ 25 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!”+ 26 Pamenepo mzimu wonyansawo unam’tsalimitsa ndipo unafuula mokweza. Kenako unatuluka mwa munthuyo.+ 27 Ataona zimenezi, anthu onse anazizwa kwambiri moti anayamba kukambirana kuti: “Kodi chimenechi n’chiyani? N’chiphunzitso chatsopano! Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu, ndipo ikumumvera.”+ 28 Chotero mbiri yake inawanda mofulumira kwambiri m’chigawo chonse cha Galileya.+

29 Nthawi yomweyo iwo anatuluka m’sunagogemo ndi kupita kunyumba kwa Simoni+ ndi Andireya. Yakobo ndi Yohane nawonso anapita nawo. 30 Koma apongozi aakazi a Simoni+ anali chigonere, akudwala malungo.*+ Mwamsanga iwo anamuuza za mayiyo. 31 Pamenepo iye anapita kumene kunali mayiyo n’kumuimiritsa, atamugwira dzanja. Atatero malungowo anatheratu+ moti mayiyo anayamba kuwatumikira.+

32 Chakumadzulo dzuwa litalowa, anthu anayamba kumubweretsera odwala onse+ ndi ogwidwa ziwanda,+ 33 ndipo anthu onse a mumzindawo anasonkhana pakhomopo. 34 Choncho Yesu anachiritsa ambiri amene anali kudwala matenda osiyanasiyana,+ ndipo anatulutsa ziwanda zambiri. Koma sanalole kuti ziwandazo zilankhule, chifukwa zinali kum’dziwa kuti ndi Khristu.+

35 M’mawa kwambiri kukali mdima, Yesu anadzuka ndi kutuluka panja, ndipo anapita kumalo kopanda anthu.+ Kumeneko anayamba kupemphera.+ 36 Koma Simoni ndi ena amene anali naye anam’funafuna 37 ndi kumupeza, ndipo anamuuza kuti: “Anthu onse akukufunafunani.” 38 Koma iye anawayankha kuti: “Tiyeni tipite kwina kumidzi yapafupi, kuti ndikalalikire+ kumenekonso, pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.”+ 39 Iye anapitadi ndipo anali kulalikira m’masunagoge mwawo mu Galileya yense ndi kutulutsa ziwanda.+

40 Kumenekonso munthu wina wakhate anafika kwa iye, ndipo anagwada pansi ndi kum’dandaulira, kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 41 Pamenepo anagwidwa chifundo,+ ndipo anatambasula dzanja lake n’kumukhudza. Kenako anamuuza kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.”+ 42 Nthawi yomweyo khate lakelo linatha, ndipo anakhala woyera.+ 43 Kenako anamupatsa malangizo amphamvu, ndi kumuuza kuti apite nthawi yomweyo. 44 Anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi, koma upite ukadzionetse kwa wansembe+ ndipo ukapereke zinthu zimene Mose analamula+ chifukwa cha kuyeretsedwa kwako, kuti zikhale umboni kwa iwo.”+ 45 Koma atachoka, munthu uja anayamba kulengeza zimenezo paliponse ndi kufalitsa nkhaniyo m’madera ena, moti Yesu sanathenso kulowa mumzinda uliwonse moonekera, koma anapitiriza kukhala kunja kopanda anthu. Komabe anthu anali kubwerabe kuchokera kumbali zonse.+

2 Koma patapita masiku angapo, analowanso mu Kaperenao ndipo anthu anamva kuti ali panyumba.+ 2 Choncho anthu ochuluka anasonkhana kumeneko, moti panalibenso malo okhala, chifukwa anthu anadzaza mpaka pakhomo, ndipo anayamba kuwauza uthenga wabwino.+ 3 Tsopano kunafika anthu anayi atanyamula munthu wakufa ziwalo ndi kubwera naye kwa iye.+ 4 Koma popeza kuti sanathe kum’fikitsa kwa Yesu chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, anasasula denga* pamene iye anali, ndipo ataboola padengapo, anatsitsirapo machira a munthu wakufa ziwalo uja.+ 5 Yesu ataona chikhulupiriro chawo,+ anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+ 6 Tsopano alembi ena anali pomwepo, ndipo anayamba kuganiza m’mitima mwawo kuti:+ 7 “N’chifukwa chiyani munthu ameneyu akulankhula chonchi? Akunyoza Mulungu ameneyu. Ndaninso wina amene angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?”+ 8 Koma nthawi yomweyo Yesu anazindikira mumtima mwake kuti iwo anali kuganiza zimenezo, ndipo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi m’mitima mwanu?+ 9 Chapafupi n’chiti, kuuza wakufa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo nyamula machira ako uyende’?+ 10 Koma kuti anthu inu mudziwe kuti Mwana wa munthu+ ali ndi mphamvu zokhululukira machimo padziko lapansi,”+ . . . anauza wakufa ziwalo uja kuti: 11 “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga machira akowa, uzipita kwanu.”+ 12 Pamenepo munthuyo anadzuka, ndipo nthawi yomweyo ananyamula machira akewo ndi kuyenda yekha pamaso pa onse,+ moti onsewo anadabwa kwambiri, ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Zoterezi sitinazionepo.”+

13 Kenako iye anapitanso m’mbali mwa nyanja. Anthu onse anakhamukira kumeneko ndipo anayamba kuwaphunzitsa. 14 Koma pamene anali kudutsa, anaona Levi+ mwana wa Alifeyo, atakhala pansi mu ofesi yokhomera msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Pamenepo Levi ananyamuka ndi kumutsatira.+ 15 Pa nthawi ina Yesu anali kudya patebulo m’nyumba ya Levi, ndipo okhometsa msonkho+ ndi ochimwa ambiri anali kudya pamodzi ndi iye ndi ophunzira ake. Kumeneko kunali anthu ambiri ndipo anayamba kumutsatira.+ 16 Koma alembi a Afarisi, ataona kuti iye akudya limodzi ndi anthu ochimwa ndi okhometsa msonkho, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Bwanji akudya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?”+ 17 Yesu atamva zimenezi anawayankha kuti: “Anthu amphamvu safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”+

18 Ophunzira a Yohane ndi Afarisi anali kusala kudya. Choncho iwo anabwera kwa iye ndi kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 19 Ndipo Yesu anawayankha kuti: “Pamene mkwati ali limodzi ndi anzake, anzake a mkwatiwo sangasale kudya,+ si choncho kodi? Chotero chifukwa chakuti mkwati ali nawo limodzi, sangasale kudya.+ 20 Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.+ 21 Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Ngati wina atachita zimenezi, mphamvu yonse ya chigambacho imakoka ndi kung’amba malayawo. Chigamba chatsopanocho chimang’amba malaya akalewo, ndipo kung’ambikako kumawonjezeka kwambiri.+ 22 Ndiponso, palibe munthu amene amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Akachita zimenezo, vinyoyo amaphulitsa matumbawo. Kenako vinyoyo amatayika ndipo matumbawo amawonongeka.+ Koma anthu amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa atsopano.”+

23 Tsopano nthawi inayake Yesu anali kudutsa m’munda wa tirigu pa tsiku la sabata. Akuyenda, ophunzira ake anayamba kubudula+ ngala za tirigu.+ 24 Pamenepo Afarisi anapita kwa iye n’kumufunsa kuti: “Taonani! N’chifukwa chiyani akuchita zosaloleka pa sabata?”+ 25 Koma Yesu anati: “Kodi simunawerengepo zimene Davide+ pamodzi ndi amuna amene anali naye anachita atamva njala, alibiretu chilichonse?+ 26 M’nkhani yonena za Abiyatara+ wansembe wamkulu, Davide analowa m’nyumba ya Mulungu ndi kudya mitanda ya mkate woonetsa+ kwa Mulungu. Anatenga mitanda ina ya mkatewo n’kupatsanso amuna amene anali naye limodzi.+ Oyenera kudya mkate umenewu ndi ansembe okha basi ndipo anthu ena onse saloledwa kudya.+ Kodi inu simunawerenge nkhani imeneyi?” 27 Chotero anapitiriza kuwauza kuti: “Sabata linakhalako chifukwa cha munthu,+ osati munthu chifukwa cha sabata.+ 28 Choncho Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa sabata.”+

3 Kachiwirinso Yesu analowa m’sunagoge. Mmenemo munali munthu wa dzanja lopuwala.+ 2 Choncho Afarisi anali kumuyang’anitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa sabata, n’cholinga chakuti amuimbe mlandu.+ 3 Ndipo iye anauza munthu wa dzanja lopuwalayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.” 4 Kenako anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiti pa sabata? Chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ Koma iwo anangokhala chete. 5 Pamenepo Yesu anawayang’ana mokwiya ndi kumva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima kwawo.+ Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhala labwinobwino.+ 6 Ataona zimenezi Afarisiwo anatuluka ndipo nthawi yomweyo anapita kukakonza chiwembu limodzi ndi a chipani cha Herode+ kuti amuphe.+

7 Koma Yesu ndi ophunzira ake anachoka ndi kupita kunyanja. Chikhamu cha anthu ochokera ku Galileya ndi ku Yudeya chinam’tsatira.+ 8 Ngakhalenso anthu ambiri ochokera ku Yerusalemu, ku Idumeya, kutsidya la Yorodano, ndi m’madera a Turo+ ndi Sidoni, anamva zonse zimene iye anali kuchita, ndipo anakhamukira kwa iye. 9 Ndipo iye anauza ophunzira ake kuti am’bweretsere ngalawa yaing’ono yoti akweremo kuti khamu la anthulo lisam’panikize. 10 Popeza kuti anali atachiritsa anthu ambiri, onse amene anali ndi matenda aakulu anali kudziponya kwa iye kuti angomukhudza.+ 11 Ngakhalenso mizimu yonyansa,+ imati ikamuona, inali kudzigwetsa pansi pamaso pake ndi kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”+ 12 Koma iye anali kuilamula mwamphamvu nthawi ndi nthawi kuti isamuulule.+

13 Kenako anakwera m’phiri ndi kuitana amene anali kuwafuna,+ ndipo iwo anapita kwa iye.+ 14 Ndiyeno anasankha gulu la anthu 12, amenenso anawatcha “atumwi,” kuti azikhala naye nthawi zonse ndi kuti aziwatuma kukalalikira+ 15 ndi kuwapatsa mphamvu zotulutsa ziwanda.+

16 Choncho m’gulu la anthu 12 amene anasankha aja munali Simoni, amene anamutchanso Petulo,+ 17 Yakobo mwana wa Zebedayo, Yohane m’bale wa Yakobo+ (awiriwa anawatchanso a Boanege, kutanthauza Ana a Bingu), 18 Andireya, Filipo, Batolomeyo, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19 ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anadzam’pereka.+

Kenako Yesu analowa m’nyumba. 20 Kumeneko khamu la anthu linasonkhananso, mwakuti sanathe n’komwe kudya chakudya.+ 21 Koma achibale+ ake atamva zimenezo, anapita kukamugwira, chifukwa anali kunena kuti: “Wachita misala.”+ 22 Komanso alembi amene anachokera ku Yerusalemu anali kunena kuti: “Ali ndi Belezebule,* ndipo amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 23 Choncho anawaitana, ndipo anayamba kuwapatsa mafanizo akuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu wagawanika, ufumu umenewo sungakhale.+ 25 Ngati nyumba yagawanika, nyumba yoteroyo singakhale.+ 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana wadziukira yekha ndipo wagawanika, sangakhale, koma akupita kokatha.+ 27 Kunena zoona, palibe amene angalowe m’nyumba ya munthu wamphamvu ndi kulanda+ katundu wake ngati sangamange munthu wamphamvuyo choyamba. Atam’manga, m’pamene angathe kutenga katundu m’nyumbamo.+ 28 Ndithu ndikukuuzani, ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya ndi machimo otani amene anachita kapena mawu onyoza otani amene analankhula.+ 29 Komabe, aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya, koma adzakhala ndi mlandu wa tchimo losatha.”+ 30 Ananena zimenezi chifukwa iwo anali kumunena kuti: “Ali ndi mzimu wonyansa.”+

31 Tsopano panafika mayi ake ndi abale ake,+ ndipo anaimirira kunja, ndi kutumiza mthenga kukamuitana.+ 32 Iye anali ndi khamu la anthu litakhala momuzungulira, ndipo anthuwo anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.”+ 33 Koma iye anawayankha kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndani?”+ 34 Kenako anayang’ana onse amene anakhala pansi momuzungulira aja, ndi kunena kuti: “Onani! Mayi anga ndi abale anga ndi awa.+ 35 Aliyense wochita chifuniro cha Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.”+

4 Tsopano Yesu anayambanso kuphunzitsa m’mphepete mwa nyanja.+ Ndipo chikhamu cha anthu chinasonkhana kwa iye, mwakuti iye anakwera ngalawa n’kupita panyanjapo ndi kukhazikika chapatali pang’ono, koma khamu lonse la anthulo linakhala m’mphepete mwa nyanjayo.+ 2 Atatero anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri+ mwa mafanizo. Powaphunzitsapo anali kuwauza kuti:+ 3 “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+ 4 Pamene anali kufesa, mbewu zina zinagwera m’mbali mwa msewu, ndipo kunabwera mbalame ndi kuzidya.+ 5 Mbewu zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira, ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+ 6 Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinawauka ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.+ 7 Mbewu zina zinagwera paminga, ndipo mingazo zinakula ndi kulepheretsa mbewuzo kukula, moti sizinabale chipatso chilichonse.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino,+ ndipo zinamera ndi kukula, mwakuti zinayamba kubala zipatso. Mbewu ina inabala zipatso 30, ina 60, ndipo ina 100.”+ 9 Kenako anawonjezera mawu akuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+

10 Tsopano pamene anakhala payekha, ena amene anali naye chapafupi limodzi ndi atumwi 12 aja, anayamba kum’funsa za mafanizo aja.+ 11 Ndipo iye anayamba kuwauza kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira chinsinsi chopatulika+ cha ufumu wa Mulungu. Koma kwa amene ali kunja zonse zimachitika mwa mafanizo,+ 12 kuti kupenya azipenya ndithu, koma osaona, ndi kuti kumva azimva ndithu, koma osazindikira tanthauzo lake, kutinso asatembenuke ndi kukhululukidwa.”+ 13 Komanso anawauza kuti: “Ngati simukumvetsa fanizo ili, ndiye mungamvetse bwanji mafanizo ena onse?

14 “Wofesayo amafesa mawu.+ 15 Chotero anthu amenewa, ndiwo mbewu zimene zimagwera m’mphepete mwa msewu kumene mawu afesedwa. Koma atangomva mawuwo, Satana amabwera+ ndi kuchotsa mawu ofesedwa mwa iwo.+ 16 Momwemonso, pali anthu amene amafesedwa pamiyala. Akangomva mawuwo, iwo amawalandira ndi chimwemwe.+ 17 Amakhala opanda mizu mwa iwo okha, ndipo amapitirizabe kwakanthawi. Koma chisautso kapena mazunzo akangobuka chifukwa cha mawuwo, iwo amapunthwa.+ 18 Ndiyeno palinso mbewu zina zofesedwa paminga. Zimenezi ndiwo anthu amene amamva mawu,+ 19 koma nkhawa+ za m’nthawi* ino, chinyengo champhamvu cha chuma,+ komanso zilakolako+ za zinthu zina, zimalowa ndi kulepheretsa mawuwo kukula, ndipo sabala zipatso.+ 20 Potsirizira pake, zimene zinafesedwa panthaka yabwino, ndiwo anthu amene amamvetsera mawu ndi kuwalandira bwino, ndipo amabala zipatso wina 30, wina 60, ndi wina 100.”+

21 Tsopano anapitiriza kuwauza kuti: “Nyale saivundikira ndi dengu loyezera zinthu kapena kuiika pansi pa bedi, amatero kodi? Koma amaiika pachoikapo nyale, si choncho kodi?+ 22 Pakuti chilichonse chobisidwa chidzaululika. Chilichonse chimene chimasungidwa mwachinsinsi kwambiri chidzadziwika.+ 23 Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+

24 Anawauzanso kuti: “Samalani zimene mukumvazi.+ Muyezo umene mukuyezera, nanunso adzakuyezerani womwewo.+ Inde, adzakuwonjezerani zochuluka.+ 25 Pakuti amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka. Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.”+

26 Iye anapitiriza kulankhula kuti: “Chotero ufumu wa Mulungu uli ngati mmene munthu amamwazira mbewu panthaka,+ 27 ndipo amagona usiku n’kumadzuka kukacha. Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma mmene zimenezi zimachitikira, mwiniwakeyo sadziwa ayi.+ 28 Pang’onopang’ono, payokha nthaka ija imabala zipatso. Choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo. 29 Koma zipatsozo zikacha, iye amamweta ndi chikwakwa, chifukwa nthawi yokolola yakwana.”

30 Iye anapitiriza kuti: “Kodi ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani? Kapena kodi tingaufotokoze ndi fanizo lotani?+ 31 Uli ngati kanjere kampiru,* kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakang’ono kwambiri mwa njere zonse za padziko lapansi+ . . . 32 koma akakafesa, kamamera ndi kukula kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo kamapanga nthambi zikuluzikulu,+ moti mbalame zam’mlengalenga+ zimatha kupeza malo okhala mumthunzi wake.”+

33 Chotero anawauza mawu mwa mafanizo ambiri+ oterewa, malinga ndi zimene akanakwanitsa kumva. 34 Ndithudi, sanalankhule nawo chilichonse popanda fanizo, koma kumbali anali kufotokoza zonse kwa ophunzira ake.+

35 Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”+ 36 Choncho atauza khamu la anthulo kuti lizipita, ophunzirawo anachoka naye pa ngalawa imene anakwera ija, koma analinso ndi ngalawa zina.+ 37 Kenako kunayamba chimphepo champhamvu chamkuntho, ndipo mafunde anali kuwomba ngalawayo, mwakuti ngalawayo inangotsala pang’ono kumira.+ 38 Koma Yesu anali kumbuyo kwa ngalawayo akugona, atatsamira pilo. Chotero anam’dzutsa ndi kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?”+ 39 Pamenepo anadzuka ndi kudzudzula mphepoyo ndi kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!”+ Chotero mphepoyo inaleka. Kenako panachita bata lalikulu.+ 40 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi? Kodi mudakali opandiratu chikhulupiriro?” 41 Koma iwo anagwidwa mantha aakulu, ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani kwenikweni, chifukwa ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera?”+

5 Kenako anafika kutsidya lina la nyanja, m’dera la Agerasa.+ 2 Tsopano atangotsika m’ngalawa, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa akuchokera m’manda achikumbutso.+ 3 Iye anali kukonda kukhala m’mandamo, ndipo n’kale lonse, kunalibe munthu ndi mmodzi yemwe, amene anatha kum’manga ngakhale ndi unyolo. 4 Izi zinali choncho chifukwa anamangidwapo mobwerezabwereza ndi matangadza ndiponso maunyolo, koma iye anali kudula maunyolowo ndi kuthyola matangadzawo. Chotero panalibe amene anatha kumugonjetsa. 5 Ndipo nthawi zonse, usiku ndi usana, anali kufuula m’manda ndi m’mapiri ndi kudzitematema ndi miyala. 6 Koma ataona Yesu chapatali ndithu, anam’thamangira ndi kum’chitira ulemu, 7 ndipo atafuula ndi mawu amphamvu,+ anati: “Kodi ndili nanu chiyani, Yesu, Mwana wa Mulungu Wam’mwambamwamba?+ Ndikukulumbiritsani+ pali Mulungu kuti musandizunze.”+ 8 Pakuti Yesu anali kuuza mzimuwo kuti: “Tuluka mwa munthuyu, mzimu wonyansa iwe.”+ 9 Ndiyeno anafunsa munthuyo kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti: “Dzina langa ndine Khamu,+ chifukwa tilipo ambiri.”+ 10 Ndipo anam’chonderera mobwerezabwereza kuti asatumize mizimuyo kutali ndi deralo.+

11 Tsopano chigulu cha nkhumba+ chinali kudya paphiri.+ 12 Chotero mizimuyo inam’chonderera kuti: “Titumizeni ku nkhumbazo, kuti tikalowe mwa zimenezo.” 13 Choncho iye anailola. Pamenepo mizimu yonyansayo inatuluka ndi kukalowa m’nkhumbazo, ndipo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi ndi kulumphira m’nyanja. Nkhumbazo zinalipo pafupifupi 2,000, ndipo zinamira m’nyanjamo imodzi ndi imodzi.+ 14 Koma amene anali kuziyang’anira anathawa ndi kukanena zimenezi mumzinda ndi m’midzi, ndipo anthu anabwera kudzaona zimene zinachitikazo.+ 15 Choncho anafika kwa Yesu, ndipo anaona munthu wogwidwa ndi chiwanda uja ali chikhalire, atavala bwino komanso maganizo ake ali bwinobwino, inde munthu uja amene anali ndi khamu la mizimu yonyansa. Pamenepo iwo anachita mantha. 16 Komanso amene anaona zochitikazo, anawafotokozera mmene zinakhalira kwa munthu wogwidwa ziwanda uja ndiponso zimene zinachitikira nkhumba zija. 17 Chotero anthuwo anayamba kuchonderera Yesu kuti achoke m’madera akwawoko.+

18 Tsopano pamene anali kukwera ngalawa, munthu amene anali ndi ziwanda uja anayamba kumuchonderera kuti aziyenda naye.+ 19 Komabe iye sanamulole, koma anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwa achibale ako,+ ndipo ukawauze zonse zimene Yehova+ wakuchitira ndi chifundo+ chimene wakusonyeza.” 20 Chotero iye anachoka ndipo anayamba kufalitsa mu Dekapole+ zonse zimene Yesu anam’chitira, moti anthu onse anadabwa kwambiri.+

21 Yesu atawolokanso pangalawa kubwerera kutsidya lina, khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye, ndipo iye anali m’mphepete mwa nyanja.+ 22 Pamenepo mmodzi wa atsogoleri a sunagoge, dzina lake Yairo, anafika. Atamuona anagwada pamapazi ake+ 23 ndi kum’chonderera mobwerezabwereza, kuti: “Mwana wanga wamkazi akudwala mwakayakaya. Chonde tiyeni mukamuike manja+ kuti achire ndi kukhala ndi moyo.”+ 24 Pamenepo ananyamuka naye limodzi, ndipo khamu lalikulu la anthu linali kumutsatira ndi kumam’panikiza.+

25 Tsopano panali mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi+ kwa zaka 12,+ 26 ndipo madokotala+ ambiri anam’chititsa kumva zopweteka zambiri. Iye anawononga chuma chake chonse koma osapindula kanthu, m’malomwake matendawo ankangokulirakulira. 27 Atamva zambiri zokhudza Yesu, anakalowa m’khamu la anthulo ndi kumudzera kumbuyo kwake, kenako anagwira+ malaya ake akunja. 28 Anachita zimenezi pakuti mumtima mwake anali kunena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”+ 29 Nthawi yomweyo kasupe wake wa magazi anauma, ndipo anamva m’thupi mwake kuti wachira nthenda yake yaikuluyo.+

30 Nthawi yomweyonso, Yesu anamva m’thupi mwake kuti mphamvu+ yatulukamo. Pamenepo anatembenuka m’khamu la anthulo ndi kufunsa kuti: “Ndani wagwira malaya angawa?”+ 31 Koma ophunzira ake anayamba kumuuza kuti: “Inunso mukuona kuti anthu onsewa akukupanikizani,+ ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndani wandigwira?’” 32 Komabe iye anali kuyang’anayang’ana kuti aone mayi amene wachita zimenezi. 33 Koma mayiyo, anachita mantha ndi kuyamba kunjenjemera, podziwa zimene zam’chitikira. Ndipo anafika pafupi n’kugwada pamaso pake ndi kumuuza zoona zonse.+ 34 Iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere,+ matenda ako aakuluwo atheretu.”+

35 Ali mkati molankhula, panafika amuna ena ochokera kunyumba kwa mtsogoleri wa sunagoge uja ndipo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira! Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.”+ 36 Koma Yesu atamva zimene anali kunenazo, anauza mtsogoleri wa sunagogeyo kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi.”+ 37 Pamenepo sanalolenso aliyense kumutsatira kupatulapo Petulo, Yakobo, ndi Yohane, m’bale wake wa Yakobo.+

38 Choncho anafika kunyumba ya mtsogoleri wa sunagoge, ndipo anamva chiphokoso cha anthu akulira ndi kubuma kwambiri. 39 Atalowa mkati, anafunsa anthuwo kuti: “N’chifukwa chiyani mukubuma ndi kulira motere? Mwana wamng’onoyu sanamwalire ayi, koma akugona.”+ 40 Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kum’seka monyodola. Koma atawatulutsa onsewo, anatenga bambo ndi mayi a mwanayo ndi amene anali naye aja, ndipo analowa kumene kunali mwanayo.+ 41 Ndiyeno anagwira dzanja la mwanayo ndi kunena kuti: “Talʹi·tha cuʹmi,” mawu amene powamasulira amatanthauza kuti: “Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!”+ 42 Nthawi yomweyo kamtsikanako kanadzuka ndi kuyamba kuyenda. Mwanayo anali ndi zaka 12. Pamenepo anthuwo anasangalala kwambiri.+ 43 Koma iye anawalamula mobwerezabwereza kuti asauze aliyense zimenezi.+ Kenako anawauza kuti apatse mtsikanayo chakudya.

6 Kenako anachoka kumeneko ndi kufika m’dera lakwawo, ndipo ophunzira ake anam’tsatira.+ 2 Sabata itafika, iye anayamba kuphunzitsa m’sunagoge. Anthu ambiri amene anali kumvetsera, anadabwa ndipo anali kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti zinthu zimenezi?+ Ndipo n’chifukwa chiyani nzeru zimenezi zinaperekedwa kwa munthu ameneyu, ndi kuti azitha kuchita ntchito zamphamvu zoterezi? 3 Kodi iyeyu si mmisiri wamatabwa,+ mwana wa Mariya,+ komanso m’bale wake wa Yakobo,+ Yosefe, Yudasi ndi Simoni?+ Ndipo alongo ake si awa omwe tili nawo pompano?” Choncho anayamba kukhumudwa naye.+ 4 Koma Yesu anapitiriza kuwauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo,+ ngakhale ndi achibale ake, ngakhale m’nyumba mwake momwe, koma kwina.”+ 5 Chotero sanathe kuchita ntchito zamphamvu zilizonse kumeneko, koma anangoika manja pa odwala owerengeka ndi kuwachiritsa. 6 Ndithudi, iye anadabwa kuona kuti anthuwo analibe chikhulupiriro. Ndipo anazungulira m’midzi yapafupi akuphunzitsa.+

7 Kenako anaitana ophunzira 12 aja, ndipo anayamba kuwatumiza awiriawiri,+ ndi kuwapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa.+ 8 Komanso, anawalangiza kuti asanyamule kanthu pa ulendowo kupatulapo ndodo yokha basi. Anawalangiza kuti asatenge mkate, thumba la chakudya,+ kapena ndalama m’zikwama zawo,+ 9 koma kuti avale nsapato, ndi kuti asavale malaya awiri amkati.+ 10 Komanso anawauza kuti: “Mukafika pakhomo lililonse,+ khalani pamenepo mpaka nthawi yochoka kumeneko itakwana.+ 11 Kulikonse kumene sakakulandirani kapena kukumvetserani, pochoka kumeneko sansani fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni kwa iwo.”+ 12 Choncho anapita ndi kukalalikira kuti anthu alape.+ 13 Kumeneko anatulutsa ziwanda zambiri,+ ndi kudzoza mafuta anthu ambiri odwala+ ndi kuwachiritsa.+

14 Tsopano izi zinamveka kwa Mfumu Herode,* chifukwa dzina la Yesu linamveka paliponse. Anthu anali kunena kuti: “Yohane m’batizi wauka kwa akufa, ndipo pa chifukwa chimenechi akuchita ntchito zamphamvu.”+ 15 Koma ena anali kunena kuti: “Ndi Eliya.”+ Ndipo ena anali kunena kuti: “Ndi mneneri monga analili aneneri ena.”+ 16 Koma Herode atamva zimenezo anayamba kunena kuti: “Ndithu Yohane amene ndinam’dula mutu uja waukitsidwadi.”+ 17 Pakuti Herodeyo anatumiza anthu kukagwira Yohane, kum’manga ndi kum’tsekera m’ndende, chifukwa Herode anakwatira Herodiya, mkazi wa m’bale wake Filipo.+ 18 Zinakhala choncho chifukwa Yohane anali kumuuza Herode mobwerezabwereza kuti: “N’kosaloleka kutenga mkazi wa m’bale wanu.”+ 19 Choncho Herodiya anam’sungira chidani mumtima+ ndipo anali kufuna kumupha, koma sanathe kutero.+ 20 Herode anali kulemekeza+ Yohane, pakuti anali kumudziwa kuti ndi munthu wolungama ndi woyera,+ choncho anali kumusunga bwino. Atamva+ zonena zake anathedwa nzeru, komabe anapitiriza kumumvetsera mokondwa.

21 Ndiyeno tsiku loyenera+ linafika pamene Herode anakonzera chakudya chamadzulo nduna zake, akuluakulu a asilikali ndi atsogoleri a mu Galileya, pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake.+ 22 Ndipo mwana wamkazi wa Herodiya analowa ndi kuvina, moti anasangalatsa Herode ndi ena amene anali kudya+ naye limodzi. Tsopano mfumu inauza mtsikanayo kuti: “Upemphe kwa ine chilichonse chimene ukufuna, ndipo ndidzakupatsa.” 23 Ndithu, anachita kumulumbirira kuti: “Chilichonse chimene ungapemphe kwa ine, ndidzachipereka kwa iwe,+ ngakhale hafu ya ufumu wangawu.”+ 24 Choncho anatuluka n’kukafunsa mayi ake kuti: “Ndikapemphe chiyani?” Mayi akewo anamuuza kuti: “Kapemphe mutu wa Yohane m’batizi.”+ 25 Nthawi yomweyo anapita kwa mfumuyo mofulumira, ndi kupempha kuti: “Ndikufuna mundipatse mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.” 26 Ngakhale kuti mfumu inamva chisoni kwambiri, sinafune kumukanira poganizira lumbiro lake lija, komanso poganizira amene anali kudya nawo chakudya patebulopo.+ 27 Choncho, nthawi yomweyo mfumu inatumiza msilikali ndi kumulamula kuti abweretse mutuwo. Iye anapita ndi kukamudula mutu m’ndendemo,+ 28 n’kuubweretsa m’mbale, ndi kuupereka kwa mtsikana uja. Ndiyeno mtsikanayo anakaupereka kwa mayi ake.+ 29 Ophunzira ake atamva zimenezo anabwera kudzatenga mtembo wake ndi kukauika m’manda achikumbutso.+

30 Tsopano atumwi anasonkhana kwa Yesu ndi kumuuza zonse zimene iwo anachita ndi kuphunzitsa.+ 31 Iye anawauza kuti: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu+ kuti mupumule pang’ono.”+ Pakuti ambiri anali kubwera ndi kupita, ndipo analibe nthawi yopuma, ngakhale yoti adye chakudya.+ 32 Choncho anakwera ngalawa, kupita kwaokhaokha kumalo opanda anthu.+ 33 Koma anthu anawaona akuchoka ndipo ambiri anadziwa zimenezo. Chotero kuchokera m’mizinda yonse, anthu anathamangira kumeneko wapansi, ndipo anthuwo ndi amene anayamba kukafika kumaloko.+ 34 Koma potsika, anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvera chifundo,+ chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Choncho anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.+

35 Tsopano kunja kunada, ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye ndi kunena kuti: “Kuno n’kopanda anthu, ndipo nthawi yatha.+ 36 Auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite m’midzi yapafupi ndi m’madera ozungulira kuti akagule okha chakudya.”+ 37 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.” Pamenepo iwo anafunsa Yesu kuti: “Kodi tipite kukagula mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari 200 ndi kuipereka kwa anthuwa kuti adye?”+ 38 Powayankha iye anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate? Pitani mukaone!” Ataiona anati: “Ilipo isanu, ndi nsomba ziwiri.”+ 39 Kenako anauza anthuwo kuti akhale m’magulu+ pa udzu wobiriwira.+ 40 Ndipo anakhaladi m’magulu, ena anthu 100, ena anthu 50.+ 41 Tsopano anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso.+ Kenako ananyemanyema+ mitanda ya mkateyo ndi kuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo, ndiponso anaduladula nsomba ziwirizo ndi kugawira anthu onsewo. 42 Choncho, anthu onsewo anadya ndi kukhuta.+ 43 Kenako anatolera zotsala ndipo zinadzaza madengu 12, osawerengera nsombazo. 44 Ndipo onse amene anadya mkatewo anali amuna okwana 5,000.+

45 Kenako mwamsanga, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti akwere ngalawa ndi kutsogola kupita kutsidya lina loyang’anizana nalo cha ku Betsaida. Koma iye anatsalira akuuza anthuwo kuti azipita kwawo.+ 46 Ndipo atatsazikana ndi anthuwo, iye anachoka n’kupita m’phiri kukapemphera.+ 47 Madzulo mdima utagwa, ngalawa ija inali pakati pa nyanja, koma iye anali yekha kumtunda.+ 48 Kenako anaona ophunzirawo akupalasa movutika,+ chifukwa anali kulimbana ndi mphepo yamphamvu. Uwu unali m’bandakucha pafupifupi pa ulonda wachinayi,* ndipo iye anawalondola akuyenda panyanja. Koma ophunzirawo anaona ngati akufuna kuwapitirira. 49 Atamuona akuyenda panyanjapo, ophunzirawo anaganiza kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!” Ndipo anafuula mokweza.+ 50 Anachita zimenezi chifukwa onsewo anamuona ndipo anavutika mumtima. Koma nthawi yomweyo iye analankhula nawo, kuti: “Limbani mtima, ndine musachite mantha.”+ 51 Pamenepo Yesu anakwera nawo m’ngalawamo, ndipo mphepoyo inaleka. Ataona izi anadabwa kwambiri mumtima mwawo.+ 52 Popeza sanamvetse tanthauzo la mitanda ya mkate ija, mitima yawo inakhalabe yosazindikira.+

53 Tsopano atawolokera kumtunda, anafika ku Genesarete ndi kuimika ngalawayo chapafupi.+ 54 Koma atangotsika m’ngalawamo, anthu anamuzindikira. 55 Choncho anthu am’dera lonselo anathamanga uku ndi uku ndi kunyamula odwala onse pamachira, kupita nawo kumene anamva kuti iye ali kumeneko. 56 Ndipo akangolowa m’midzi, kapena m’mizinda, kapena m’madera ozungulira alionse,+ anthu anali kukhazika odwala m’misika. Iwo anali kum’dandaulira kuti angogwira+ chabe ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake+ akunja. Ndipo anthu ambiri anaugwira ndi kuchira.+

7 Tsopano Afarisi ndi alembi ena ochokera ku Yerusalemu anasonkhana kwa Yesu.+ 2 Ndipo pamene anaona ena mwa ophunzira ake akudya chakudya ndi manja oipitsidwa, kapena kuti, m’manja mosasamba*+  . . .  3 pakuti Afarisi ndi Ayuda onse sadya osasamba m’manja mpaka m’zigongono, posunga mwambo wa makolo. 4 Akabwera kuchokera kumsika, sadya mpaka atadziyeretsa mwa kudziwaza madzi. Palinso miyambo ina yambiri+ imene anailandira ndipo akuisunga, monga kuviika makapu, mitsuko ndi ziwiya zamkuwa m’madzi+ . . . 5 choncho Afarisi ndi alembi amenewa anam’funsa iye kuti: “N’chifukwa chiyani ophunzira anu satsatira miyambo ya makolo, koma amadya chakudya ndi manja oipitsidwa?”+ 6 Iye anawayankha kuti: “Yesaya analosera moyenera za anthu onyenga inu, monga mmene Malemba amanenera kuti,+ ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo ili kutali ndi ine.+ 7 Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’+ 8 Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu, ndi kuumirira mwambo wa anthu.”+

9 Pamenepo anapitiriza kuwauza kuti: “Mochenjera, mumakankhira pambali malamulo+ a Mulungu kuti musunge mwambo wanu. 10 Mwachitsanzo, Mose ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,’+ komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+ 11 Koma anthu inu mumanena kuti, ‘Munthu akauza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ine ndili nacho, chimene mukanatha kupindula nacho, ndi khobani,+ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa+ kwa Mulungu,)”’ . . . 12 anthu inu simulolanso munthuyo kuchitira bambo ake kapena mayi ake chinthu chilichonse.+ 13 Mwa kuchita zimenezi, mumapangitsa mawu a Mulungu+ kukhala opanda pake chifukwa cha mwambo wanu umene munaupereka kwa anthu. Ndipo mumachita zinthu zambiri+ zofanana ndi zimenezi.” 14 Atatero, anaitananso khamu la anthuwo kuti abwere kwa iye, ndipo anayamba kulankhula nawo kuti: “Mverani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.+ 15 Palibe chilichonse chochokera kunja kwa munthu ndi kulowa m’thupi mwake chimene chingaipitse munthu, koma zotuluka mwa munthu ndi zimene zimaipitsa munthu.”+ 16* ——

17 Tsopano atalowa m’nyumba ina kutali ndi khamu la anthulo, ophunzira ake anayamba kumufunsa za fanizo lija.+ 18 Chotero iye anawafunsa kuti: “Kodi nanunso ndinu osazindikira ngati iwo aja?+ Kodi inunso simudziwa kuti palibe chochokera kunja kwa thupi n’kudutsa m’thupi mwa munthu chimene chingamuipitse, 19 popeza sichidutsa mumtima mwake, koma m’matumbo mwake, ndipo chimakatuluka kuchimbudzi?”+ Pamenepo anagamula kuti zakudya zonse n’zoyera.+ 20 Kenako anafotokozanso kuti: “Chotuluka mwa munthu n’chimene chimaipitsa munthu.+ 21 Pakuti mkatimo, mumtima mwa munthu,+ mumatuluka maganizo oipa. Mumatuluka zadama,*+ zakuba, zaumbanda,+ 22 zachigololo, kusirira kwa nsanje,+ kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lotayirira,+ diso la kaduka, mnyozo, kudzikweza, ndiponso kuchita zinthu mosaganizira ena. 23 Zoipa zonsezi zimatuluka mkatimo ndipo zimaipitsa munthu.”+

24 Atanyamuka kumeneko, analowera kumadera a Turo ndi Sidoni.+ Kumeneko anakalowa m’nyumba ina, ndipo sanafune kuti aliyense adziwe kuti ali kumeneko. Koma anthu anadziwabe.+ 25 Nthawi yomweyo, mayi wina amene anali ndi mwana wamkazi wogwidwa ndi mzimu wonyansa anamva za iye ndipo anabwera ndi kugwada, n’kumuweramira mpaka nkhope yake pansi.+ 26 Mayiyu anali Mgiriki, wachisurofoinike. Iye anapempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wakeyo.+ 27 Koma Yesu anayamba n’kunena kuti: “Choyamba, zimafunika kuti ana akhute kaye, chifukwa si bwino kutenga chakudya cha ana+ ndi kuponyera tiagalu.”+ 28 Koma poyankha mayiyo ananena kuti: “Inde mbuyanga, komabe tiagalu timadya nyenyeswa+ za anawo pansi pa tebulo.”+ 29 Yesu atamva mawuwo anauza mayiyo kuti: “Chifukwa wanena zimenezi, pita, chiwandacho chatuluka mwa mwana wakoyo.”+ 30 Choncho anapita kunyumba kwake ndipo anakapeza+ mwanayo atagona pabedi chiwandacho chitatuluka.

31 Tsopano pobwerera kuchoka m’madera a Turo, anadutsa ku Sidoni ndi kufika kunyanja ya Galileya mpaka kukadutsa mkati mwa zigawo za Dekapole.+ 32 Kumeneko anthu anam’bweretsera munthu wogontha komanso wovutika kulankhula. Iwo anamupempha kuti aike dzanja lake pa munthuyo.+ 33 Koma iye anatenga munthuyo ndi kuchoka naye pakhamu la anthulo kupita naye pambali. Kumeneko anapisa zala zake m’makutu a munthuyo, ndipo analavula ndi kukhudza lilime lake.+ 34 Pamenepo anayang’ana kumwamba,+ kenako anausa moyo*+ ndi kumuuza kuti: “Efata,” kutanthauza kuti, “Tseguka.” 35 Atatero, makutu ake anatseguka,+ lilime lake lomangikalo linamasuka, moti anayamba kulankhula bwinobwino. 36 Ndiyeno anawalamula kuti asauze aliyense zimenezo.+ Koma ankati akawaletsa mwamphamvu kuti asauze aliyense, m’pamenenso iwo anali kuzifalitsa kwambiri.+ 37 Inde, iwo anali kudabwa kwambiri+ ndipo anali kunena kuti: “Wachita zinthu zonse bwinobwino ndithu. Ngakhale ogontha akumva ndipo osalankhula akuwalankhulitsa.”+

8 M’masiku amenewo, khamu la anthu linasonkhananso, koma linalibe chakudya. Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake ndi kuwauza kuti:+ 2 “Khamu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine masiku atatu tsopano ndipo alibe chakudya. 3 Koma ndikawauza kuti azipita kwawo ndi njala, alenguka panjira. Ndipo ena a iwo achokera kutali kwambiri.” 4 Pamenepo ophunzira ake anamuyankha kuti: “Munthu angaipeze kuti mitanda ya mkate yokwanira kudyetsa anthu onsewa kutchire ngati kuno?”+ 5 Koma iye anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7.”+ 6 Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako, anatenga mitanda 7 ya mkate ija, ndi kuyamika.+ Atatero anainyemanyema n’kupatsa ophunzira ake kuti agawe, ndipo iwo anagawira khamu la anthulo.+ 7 Ophunzirawo analinso ndi tinsomba towerengeka ndipo atadalitsa tinsombato, anawauza kuti agawirenso anthu tinsombato.+ 8 Chotero anthuwo anadya ndi kukhuta, moti anatolera zotsala zodzaza madengu akuluakulu 7.+ 9 Komatu panali amuna pafupifupi 4,000. Pambuyo pake anawauza kuti azipita.+

10 Nthawi yomweyo iye anakwera ngalawa pamodzi ndi ophunzira ake ndi kufika m’madera a Dalamanuta.+ 11 Kumeneku kunafika Afarisi ndipo anayamba kutsutsana naye. Ankafuna kuti iye awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba, pofuna kumuyesa.+ 12 Choncho anadzuma mowawidwa mtima+ ndi kunena kuti: “N’chifukwa chiyani m’badwo umenewu ukufunitsitsa chizindikiro? Ndithu ndikukuuzani, M’badwo umenewu sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse.”+ 13 Atatero anawasiya, ndi kukweranso ngalawa kupita kutsidya lina.

14 Komano iwo anaiwala kutenga mikate, chotero analibe chilichonse m’ngalawamo koma mtanda wa mkate umodzi wokha basi.+ 15 Ndipo anayamba kuwachenjeza mwamphamvu kuti: “Khalani maso! Chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.”+ 16 Choncho ophunzirawo anayamba kukangana pa nkhani yosowa mkate.+ 17 Yesu poona zimenezo, anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana nkhani yosowa mikate?+ Kodi simukuzindikira ndi kumvetsa tanthauzo lake mpaka pano? Kodi mitima yanu ikadali yosazindikira?+ 18 ‘Ngakhale kuti muli maso, kodi simuona? Ndipo ngakhale kuti muli ndi makutu kodi simumva?’+ Komanso simukukumbukira kodi, 19 kuchuluka kwa madengu a zotsala zimene munatolera, pamene ndinanyemanyema mitanda isanu ya mkate+ koma n’kukwanira amuna 5,000?” Iwo anayankha kuti: “Anali madengu 12.”+ 20 “Pamene ndinanyemanyema mitanda 7 ya mkate koma inakwanira amuna 4,000, kodi munatolera madengu akuluakulu angati a zotsala?” Iwo anamuyankha kuti: “Analipo 7.”+ 21 Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Kodi simukumvetsabe tanthauzo lake?”+

22 Tsopano anafika ku Betsaida. Kumeneku anthu anamubweretsera munthu wakhungu. Anthuwo anamuchonderera kuti akhudze+ munthuyo. 23 Iye anagwira dzanja la munthu wakhunguyo, ndi kupita naye kunja kwa mudzi. Kumeneko iye analavulira+ m’maso mwake, ndi kuika manja ake pa munthuyo ndi kumufunsa kuti: “Kodi ukuona chilichonse?” 24 Munthuyo anayang’ana m’mwamba ndi kunena kuti: “Ndikuona anthu, chifukwa ndikuona zinthu zooneka ngati mitengo, koma zikuyendayenda.” 25 Pamenepo anagwiranso m’maso mwa munthuyo. Munthuyo anayamba kuona bwinobwino, chifukwa anam’chiritsa, moti anayamba kuona chilichonse bwinobwino. 26 Kenako anamuuza kuti azipita kwawo, ndi kunena kuti: “Koma usalowe m’mudzimu.”+

27 Tsopano Yesu ndi ophunzira ake anachoka ndi kupita kumidzi ya Kaisareya wa Filipi. Ali m’njira, anayamba kufunsa ophunzira ake, kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 28 Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane M’batizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumati Mmodzi wa aneneri.”+ 29 Ndiyeno anafunsa ophunzirawo kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Poyankha, Petulo ananena kuti: “Ndinu Khristu.”+ 30 Pamenepo anawaletsa mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye.+ 31 Kenako, anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri. Iye adzakanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa,+ koma adzauka patapita masiku atatu.+ 32 Ndithudi, iye analankhula mawu amenewa molimba mtima. Koma Petulo anam’tengera pambali ndi kuyamba kum’dzudzula.+ 33 Pamenepo Yesu anatembenuka, ndi kuyang’ana ophunzira ake, kenako anakalipira Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”+

34 Kenako iye anaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo,* ndi kunditsatira mosalekeza.+ 35 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine ndi uthenga wabwino, adzaupulumutsa.+ 36 Kunena zoona, pali phindu lanji ngati munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?+ 37 N’chiyani kwenikweni chimene munthu angapereke chosinthanitsa ndi moyo wake?+ 38 Pakuti aliyense wochita manyazi ndi ine, komanso ndi mawu anga mu m’badwo wachigololo ndi wochimwa uno, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi+ akadzafika mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo oyera.”+

9 Ndiye anawauzanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe, kufikira choyamba ataona ufumu wa Mulungu utabwera ndi mphamvu zake.”+ 2 Malinga ndi zimenezo, patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane, n’kukwera nawo m’phiri lalitali, kwaokhaokha. Kumeneko iye anasandulika pamaso pawo,+ 3 mwakuti malaya ake akunja ananyezimira, n’kuyera kwambiri kuposa mmene wochapa zovala aliyense padziko lapansi angayeretsere zovala.+ 4 Komanso, Eliya ndi Mose anaonekera kwa iwo, ndipo anali kukambirana ndi Yesu.+ 5 Petulo ataona zimenezi anauza Yesu kuti: “Rabi, ndi bwino ife tizikhala pano, choncho timange mahema atatu pano, limodzi lanu, limodzi la Mose, ndi lina la Eliya.”+ 6 Petulo sanadziwe choti anene, chifukwa ophunzirawo anachita mantha kwambiri. 7 Pamenepo kunachita mtambo ndipo unawaphimba. Kenako mumtambomo munatuluka mawu+ akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga+ wokondedwa, muzimumvera.”+ 8 Pamenepo iwo anayang’ana uku ndi uku, ndipo anangoona kuti palibe wina aliyense, koma Yesu yekha basi.+

9 Pamene anali kutsika m’phirimo, Yesu anawalangiza mwamphamvu kuti asauze+ aliyense zimene anaonazo, kufikira Mwana wa munthu atauka kwa akufa.+ 10 Iwo anasungadi zimenezo mumtima, koma anayamba kukambirana tanthauzo la kuuka kwa akufa kumeneku. 11 Tsopano anayamba kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya+ ayenera kubwera choyamba?”+ 12 Iye anawayankha kuti: “Eliya adzabweradi choyamba ndi kubwezeretsa zinthu zonse.+ Koma n’chifukwa chiyani malemba amanena za Mwana wa munthu, kuti ayenera kukumana ndi mavuto ambiri,+ ndi kumuchita zinthu ngati munthu wopanda pake?+ 13 Kunena za kubwera kwa Eliya,+ ine ndikukuuzani kuti iye anabwera kale, ndipo anam’chitira zilizonse zimene anafuna, mmenedi Malemba amanenera za iye.”+

14 Tsopano atayandikira kumene kunali ophunzira ena aja, iwo anaona khamu lalikulu la anthu litawazungulira, ndipo alembi anali kukangana nawo.+ 15 Koma khamu lonselo litamuona linadabwa, ndipo linam’thamangira ndi kuyamba kum’patsa moni. 16 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Mukukangana nawo chiyani?” 17 Wina m’khamulo anamuyankha kuti: “Mphunzitsi, ine ndabweretsa mwana wanga wamwamuna kwa inu chifukwa ali ndi mzimu womulepheretsa kulankhula.+ 18 Mzimuwo umati ukamugwira, umamugwetsera pansi. Akatero amachita thovu ndi kukukuta mano, ndipo amatha mphamvu. Chotero, ndinauza ophunzira anu kuti autulutse, koma alephera.”+ 19 Poyankha iye anawauza kuti: “Inu a m’badwo wopanda chikhulupiriro,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.”+ 20 Pamenepo iwo anapita naye kwa Yesu. Koma mzimuwo utamuona, nthawi yomweyo unatsalimitsa mwanayo. Atagwa pansi anagubudukagubuduka ndi kuchita thovu.+ 21 Ndiyeno anafunsa bambo ake kuti: “Izi zakhala zikumuchitikira kwa nthawi yaitali bwanji?” Bamboyo anati: “Kuyambira ali mwana, 22 mwakuti nthawi zambiri wakhala ukum’gwetsera pamoto ndi m’madzi kuti umuwononge.+ Koma ngati mungathe kuchitapo kanthu, tichitireni chifundo ndi kutithandiza.” 23 Yesu anafunsa bamboyo kuti: “Mukuti, ‘Ngati mungathe’? Chilichonsetu n’chotheka kwa aliyense ngati iyeyo ali ndi chikhulupiriro.”+ 24 Nthawi yomweyo bambo wa mwanayo anafuula ndi kunena kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho! Limbitsani chikhulupiriro changa!”+

25 Tsopano Yesu ataona kuti gulu la anthu likukhamukira kwa iwo, anakalipira+ mzimu wonyansawo kuti: “Mzimu wosalankhulitsa ndi wogonthetsa iwe, ndikukulamula, tuluka ndipo usadzalowenso mwa iye.” 26 Choncho mwanayo atafuula ndi kutsalima kwambiri, mzimuwo unatuluka.+ Iye anangokhala ngati wafa, mwakuti anthu ambiri anali kunena kuti: “Wamwalira!” 27 Koma Yesu anamugwira dzanja ndi kumudzutsa, ndipo anaimirira.+ 28 Tsopano atalowa m’nyumba, ophunzira ake anayamba kumufunsa paokha kuti: “N’chifukwa chiyani ife tinalephera kuutulutsa?”+ 29 Iye anawayankha kuti: “Mzimu wa mtundu umenewu sungathe kutuluka ndi chilichonse, koma pemphero basi.”+

30 Atachoka kumeneko anapitiriza ulendo wawo kudutsa mu Galileya, koma iye sanafune kuti aliyense adziwe zoti ali kumeneko. 31 Pakuti anali kuphunzitsa ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzamupha,+ koma ngakhale adzamuphe, adzauka patapita masiku atatu.”+ 32 Ophunzirawo sanali kumvetsa mawuwa, ndipo anali kuopa kumufunsa.+

33 Kenako anafika ku Kaperenao. Ndiyeno pamene anali m’nyumba anawafunsa kuti: “Munali kukangana chiyani m’njira?”+ 34 Iwo anangokhala chete, pakuti m’njira anali kukangana za amene ali wamkulu pakati pawo.+ 35 Choncho anakhala pansi ndi kuitana ophunzira 12 aja ndi kuwauza kuti: “Ngati aliyense akufuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza pa onse, ndiponso mtumiki wa onse.”+ 36 Tsopano anatenga mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo, ndi kumukumbatira, ndipo anawauza kuti:+ 37 “Aliyense wolandira mmodzi wa ana aang’ono oterewa m’dzina langa, walandiranso ine. Ndipo aliyense wolandira ine, salandira ine ndekha, koma amalandiranso iye amene anandituma.”+

38 Kenako Yohane anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ife taona munthu wina akutulutsa ziwanda m’dzina lanu, choncho tinamuletsa,+ chifukwa sanali kuyenda ndi ife.”+ 39 Koma Yesu anati: “Musamuletse, chifukwa palibe amene adzachita ntchito zamphamvu m’dzina langa, ndi kundinenera zachipongwe mwamsanga.+ 40 Pakuti amene sakutsutsana ndi ife ali kumbali yathu.+ 41 Chifukwa aliyense wokupatsani kapu+ ya madzi akumwa chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu,+ ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika ayi. 42 Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana tokhulupirirati, zingakhale bwino kwambiri kuti amumangirire chimwala champhero m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kumuponya m’nyanja.+

43 “Ndipo ngati dzanja lako limakuphunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi, kusiyana n’kupita ku Gehena,* kumoto umene sungazimitsidwe, uli ndi manja onse awiri.+ 44* —— 45 Ndipo ngati phazi lako limakupunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli wolumala,+ kusiyana n’kuponyedwa m’Gehena uli ndi mapazi onse awiri.+ 46* —— 47 Ngati diso lako limakuchimwitsa, ulitaye.+ Ndi bwino kuti ulowe mu ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana n’kuponyedwa mu Gehena uli ndi maso onse awiri,+ 48 kumene mphutsi za mitembo sizifa ndipo moto wake suzima.+

49 “Pakuti aliyense ayenera kuwazidwa mchere+ umene ukuimira moto. 50 Mchere ndi wabwino, koma mcherewo ukatha mphamvu, kodi mungaibwezeretse bwanji?+ Khalani ndi mchere+ mwa inu nokha, ndipo sungani mtendere+ pakati panu.”

10 Atachoka kumeneko anakafika kumadera a kumalire kwa Yudeya kutsidya la Yorodano. Kumenekonso khamu la anthu linasonkhananso kwa iye, ndipo mwachizolowezi chake anayamba kuwaphunzitsa.+ 2 Tsopano kunafika Afarisi. Pofuna kumuyesa, anayamba kumufunsa ngati n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake.+ 3 Poyankha iye anawafunsa kuti: “Kodi Mose anakulamulani chiyani?” 4 Iwo anati: “Mose analola kuti munthu akafuna kusiya mkazi wake azilemba kalata yothetsa ukwati ndi kum’siya mkaziyo.”+ 5 Koma Yesu anawauza kuti: “Iye anakulemberani lamulo limeneli chifukwa cha kuuma mtima kwanuku.+ 6 Koma kuyambira pa chiyambi pa chilengedwe, ‘Mulungu anawalenga mwamuna ndi mkazi.+ 7 Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, 8 ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi,’+ moti salinso awiri, koma thupi limodzi. 9 Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”+ 10 Pamenenso anali m’nyumba,+ ophunzira anayamba kumufunsa za nkhani imeneyi. 11 Iye anawauza kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo+ molakwira mkaziyo. 12 Ndipo ngati mkazi wasiya mwamuna wake, ndiyeno n’kukwatiwa ndi wina, wachita chigololo.”+

13 Tsopano anthu anayamba kum’bweretsera ana aang’ono kuti awakhudze ndi manja ake, koma ophunzirawo anawakalipira.+ 14 Ataona zimenezi Yesu anakwiya ndipo anawauza kuti: “Alekeni anawo abwere kwa ine, musawaletse ayi. Pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.+ 15 Ndithu ndikukuuzani, Aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa n’komwe mu ufumuwo.”+ 16 Ndiyeno anatenga anawo m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa, mwa kuika manja ake pa iwo.+

17 Tsopano pamene anali kupita, mwamuna wina anam’thamangira ndi kugwada pamaso pake. Kenako anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 18 Yesu anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino?+ Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+ 19 Iwe umadziwa malamulo akuti, ‘Usaphe munthu,*+ Usachite chigololo,+ Usabe,+ Usapereke umboni wonama,+ Usachite chinyengo+ ndiponso lakuti Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’”+ 20 Pamenepo munthuyo anayankha kuti: “Mphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamng’ono.” 21 Yesu anamuyang’ana ndipo anam’konda. Kenako anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22 Koma iye anakhumudwa atamva mawuwo, ndipo anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+

23 Yesu anayang’ana uku ndi uku, kenako anauza ophunzira akewo kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu andalama+ adzalowe mu ufumu wa Mulungu!”+ 24 Koma ophunzirawo anadabwa+ nawo mawu akewa. Poyankha Yesu anabwerezanso kuti: “Ana inu, kulowa mu ufumu wa Mulungu n’kovuta kwambiri! 25 N’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”+ 26 Pamenepo iwo anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndani?”+ 27 Yesu anawayang’ana ndi kuwauza kuti: “Kwa anthu n’zosathekadi, koma sizili choncho kwa Mulungu, pakuti zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.”+ 28 Petulo anayamba kumuuza kuti: “Onani! Ife tinasiya zinthu zonse ndipo takhala tikukutsatirani.”+ 29 Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani amuna inu, Palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino,+ 30 amene panopa sadzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100+ m’nthawi* ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, limodzi ndi mazunzo,+ ndipo m’nthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha. 31 Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza, ndipo omaliza adzakhala oyamba.”+

32 Tsopano anapitiriza ulendo wawo wopita ku Yerusalemu. Yesu anali patsogolo pawo, ndipo iwo anadabwa kwambiri. Anthu amene anali kum’tsatirawo anayamba kuchita mantha. Pamenepanso anatengera pambali ophunzira 12 aja ndi kuyamba kuwauza zinthu izi zimene zinali pafupi kum’chitikira:+ 33 “Tsopano kumene tikupitaku ndi ku Yerusalemu. Kumeneku Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo akamuweruza kuti aphedwe, ndipo akam’pereka kwa anthu amitundu.+ 34 Iwo akam’chitira chipongwe, kum’lavulira, kum’kwapula ndi kumupha, koma patapita masiku atatu, adzauka.”+

35 Koma Yakobo ndi Yohane, ana aamuna awiri a Zebedayo,+ anapita kwa iye ndi kumuuza kuti: “Mphunzitsi, tikufuna mutichitire chimene tikupempheni.”+ 36 Iye anawafunsa kuti: “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?” 37 Iwo anamuyankha kuti: “Mutilole kuti mmodzi wa ife adzakhale kudzanja lanu lamanja, ndipo wina adzakhale kumanzere kwanu mu ulemerero wanu.”+ 38 Koma Yesu anawauza kuti: “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwa zimene ine ndikumwa, kapena kubatizidwa ubatizo umene ine ndikubatizidwa nawo?”+ 39 Iwo anayankha kuti: “Tingathe.” Pamenepo Yesu anawauza kuti: “Zimene ine ndikumwa mudzamwadi, ndipo mudzabatizidwadi ndi ubatizo umene ine ndikubatizidwa nawo.+ 40 Koma kunena zokhala kudzanja langa lamanja kapena lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo,+ koma Atate wanga adzaupereka kwa anthu amene iwo anawakonzera.”

41 Tsopano ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndi Yakobo ndi Yohane.+ 42 Koma Yesu anawaitana, ndipo atafika kwa iye, anawauza kuti: “Inu mukudziwa kuti amene amaoneka ngati akulamulira anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu awo amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 43 Sizili choncho pakati panu. Koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu.+ 44 Amene akufuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wa onse.+ 45 Pakuti ngakhale Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa,+ koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo+ kuwombola anthu ambiri.”+

46 Kenako anafika mu Yeriko. Koma pamene iye ndi ophunzira ake ndi gulu lalikulu ndithu anali kutuluka mu Yeriko, Batimeyu, wopemphapempha komanso wakhungu (mwana wa Timeyu), anakhala pansi m’mphepete mwa msewu.+ 47 Pamene anamva kuti ndi Yesu Mnazareti, Batimeyu anayamba kufuula kuti: “Mwana wa Davide,+ Yesu, ndichitireni chifundo!”+ 48 Pamene ambiri anali kumuuza mwamphamvu kuti akhale chete, m’pamenenso iye anafuula kwambiri kuti: “Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!”+ 49 Choncho, Yesu anaima ndi kunena kuti: “Muitaneni.” Iwo anaitana wakhunguyo, ndi kumuuza kuti: “Limba mtima, nyamuka, akukuitana.”+ 50 Pamenepo anaponya uko malaya ake akunja, ndipo ananyamuka mofulumira kupita kwa Yesu. 51 Tsopano poyankha Yesu anamufunsa kuti: “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”+ Wakhunguyo anayankha kuti: “Rab·boʹni, ndithandizeni ndiyambe kuona.”+ 52 Yesu anamuuza kuti: “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Nthawi yomweyo anayamba kuona,+ ndipo anayamba kutsatira Yesu mumsewu.+

11 Tsopano pamene anali kuyandikira Yerusalemu, Betefage ndi Betaniya,+ ali paphiri la Maolivi, anatumiza ophunzira ake awiri+ 2 ndi kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi umene mukuuonawo. Mukakalowa mmenemo, mukapeza bulu wamng’ono wamphongo atam’mangirira, amene munthu sanakwerepo chiyambire. Mukam’masule ndi kubwera naye kuno.+ 3 Wina akakakufunsani kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukumumasula?’ Mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna, ndipo akangotha kum’gwiritsa ntchito am’bweza nthawi yomweyo.’”+ 4 Choncho anapita ndipo anapeza bulu wamphongo atam’mangirira pakhomo, m’mphepete mwa msewu waung’ono. Chotero iwo anamasula buluyo.+ 5 Koma ena mwa anthu amene anali ataimirira chapomwepo anayamba kuwafunsa kuti: “Cholinga chanu n’chiyani pomasula buluyu?”+ 6 Iwo anawauza monga mmene Yesu ananenera ndipo anawalola kuti apite.+

7 Choncho anabweretsa bulu+ uja kwa Yesu. Kenako anayala malaya awo akunja pabuluyo, ndipo iye anakwerapo.+ 8 Komanso, anthu ambiri anayala malaya awo akunja+ mumsewu, koma ena anadula zitsamba+ m’minda.+ 9 Ndiyeno amene anali patsogolo ndi amene anali kubwera m’mbuyo anali kufuula kuti: “M’pulumutseni!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!+ 10 Wodalitsidwa ufumu ukubwerawo wa atate wathu Davide!+ M’pulumutseni kumwambamwambako!” 11 Pamenepo analowa mu Yerusalemu, ndi kufika m’kachisi. Ndiyeno anayang’anayang’ana zinthu zonse, koma popeza nthawi inali itatha kale, anapita ku Betaniya limodzi ndi ophunzira ake 12 aja.+

12 Tsiku lotsatira, atatuluka mu Betaniya, anamva njala.+ 13 Ndipo ali chapatali ndithu, anaona mkuyu umene unali ndi masamba. Iye anapita pomwepo kuti akaone ngati angapezemo kanthu. Koma atafika pamtengowo, sanapezemo chilichonse koma masamba okha basi, pakuti sinali nyengo ya nkhuyu.+ 14 Choncho iye anauza mtengowo kuti: “Munthu sadzadyanso zipatso zako kwamuyaya.”+ Ndipo ophunzira ake anali kumvetsera.

15 Tsopano anafika ku Yerusalemu. Kumeneko analowa m’kachisi n’kuyamba kuthamangitsa ogula ndi ogulitsa m’kachisimo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndiponso mabenchi a ogulitsa nkhunda.+ 16 Iye sanalole aliyense kudutsa m’kachisimo atanyamula katundu. 17 Ndiyeno anayamba kuphunzitsa ndi kunena kuti: “Kodi Malemba sanena kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo+ mitundu yonse’?+ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+ 18 Ansembe aakulu ndi alembi anamva zimenezo, ndipo anayamba kufunafuna njira yomuphera,+ chifukwa anali kumuopa, pakuti khamu lonse la anthu nthawi zonse linali kudabwa ndi zimene anali kuphunzitsa.+

19 Tsopano chakumadzulo pa tsikulo, iwo anatuluka mumzindawo. 20 Koma pamene anali kudutsa m’mamawa, anaona mkuyu uja utafota kale ndi mizu yomwe.+ 21 Choncho Petulo, pokumbukira ananena kuti: “Rabi, onani! mkuyu umene munautemberera uja wafota.”+ 22 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. 23 Ndithu ndikukuuzani kuti aliyense wouza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano udziponye m’nyanja,’ ndipo sakukayika mumtima mwake, koma ali ndi chikhulupiriro kuti zimene wanena zichitikadi, zidzaterodi.+ 24 N’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Pa zinthu zonse zimene mukupempherera ndi kupempha, khalani ndi chikhulupiriro ngati kuti mwazilandira kale, ndipo mudzazilandiradi.+ 25 Ndipo mukaimirira n’kumapemphera,+ khululukani chilichonse chimene wina anakulakwirani kuti Atate wanu wakumwamba akukhululukireni machimo anunso.”+ 26* ——

27 Kenako anafikanso ku Yerusalemu. Koma pamene anali kuyenda m’kachisi, ansembe aakulu, alembi ndi akulu anabwera kwa iye.+ 28 Iwo anayamba kum’funsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndani anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 29 Yesu anawauza kuti: “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zinthu zimenezi.+ 30 Kodi ubatizo+ wa Yohane unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu? Ndiyankheni.”+ 31 Pamenepo iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye anena kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+ 32 Koma nanga tinganene kuti ‘Unachokera kwa anthu’ ngati?” . . . Anali kuopa khamu la anthu, chifukwa anthu onsewo anali kukhulupirira kuti Yohane analidi mneneri.+ 33 Ndiyeno poyankha kwa Yesu anangoti: “Sitikudziwa.” Nayenso Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”+

12 Kenako, anayamba kulankhula nawo m’mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa, ndi kumanga nsanja.+ Atatero anausiya m’manja mwa alimi+ n’kupita kudziko lina.+ 2 Tsopano nyengo ya zipatso itakwana, iye anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akam’patseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo.+ 3 Koma iwo anam’gwira, n’kumumenya ndi kum’bweza chimanjamanja.+ 4 Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema m’mutu ndi kumuchitira zachipongwe.+ 5 Anatumizanso wina, koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha. 6 Tsopano anatsala ndi mmodzi yekha, mwana wake wokondedwa.+ Anatumizanso mwanayo kwa iwo ngati wotsirizira, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’+ 7 Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’+ 8 Choncho anamugwira n’kumupha,+ ndipo anamuponya kunja kwa munda wa mpesawo.+ 9 Kodi mwinimunda wa mpesawo adzachita chiyani? Adzabwera ndi kupha alimiwo, ndipo munda wa mpesawo+ adzaupereka kwa ena.+ 10 Kodi simunawerengepo lemba limene limati, ‘Mwala+ umene omanga nyumba anaukana, umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri’?+ 11 Kodi simunawerenge kuti ‘Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?”+

12 Atamva zimenezo anayamba kufunafuna njira yomugwirira, koma anaopa khamu la anthu, pakuti iwo anazindikira kuti iye ananena fanizolo akuganiza za iwowo. Choncho anangomusiya n’kuchokapo.+

13 Pambuyo pake anam’tumizira ena mwa Afarisi ndi a chipani cha Herode,+ kuti akam’kole m’mawu ake.+ 14 Atafika, iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo simusamala kuti uyu ndani, chifukwa simuyang’ana maonekedwe a munthu, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi:+ Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi tizipereka kapena tisamapereke?”+ Pozindikira chinyengo chawo, Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mukundiyesa? Bweretsani khobidi la dinari kuno ndilione.”+ 16 Iwo anam’patsadi. Ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi chifaniziro ichi ndi mawu akewa n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”+ 17 Pamenepo Yesu anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.”+ Ndipo iwo anadabwa naye kwambiri.+

18 Kenako Asaduki amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa iye ndipo anam’funsa kuti:+ 19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati munthu wamwalira ndi kusiya mkazi koma osasiya mwana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.+ 20 Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma pomwalira, sanasiye mwana aliyense.+ 21 Wachiwiri anatenga mkaziyo, koma nayenso anamwalira osasiya mwana. Zimenezi zinachitikanso chimodzimodzi kwa wachitatu. 22 Ndipo onse 7 aja sanasiye mwana. Pamapeto pake mkazi nayenso anamwalira.+ 23 Kodi pouka kwa akufa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anam’kwatira.”+ 24 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu?+ 25 Akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 26 Koma zakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?+ 27 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.”+

28 Tsopano mmodzi wa alembi amene anafika ndi kuwamva akutsutsana, anadziwa kuti anawayankha bwino, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo loyamba ndi liti pa malamulo onse?”+ 29 Yesu anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova* Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.+ 30 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’+ 31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” 32 Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi, ndipo palibenso wina, koma Iye yekha.’+ 33 Kunena za kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse, komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.”+ 34 Pamenepo Yesu, pozindikira kuti wayankha mwanzeru, anauza mlembiyo kuti: “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo panalibe amene analimba mtima kumufunsanso.+

35 Koma pamene Yesu anali kuphunzitsa m’kachisi, anayankha zonse mwa kufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 36 Mwa mzimu woyera,+ Davideyo ananena kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’+ 37 Davideyo anamutcha kuti ‘Ambuye,’ nanga zikutheka bwanji kuti alinso mwana wake?”+

Ndipo khamu lalikulu linali kumumvetsera mosangalala.+ 38 Pophunzitsapo Yesu ananenanso kuti: “Chenjerani ndi alembi+ amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ndi kupatsidwa moni m’misika. 39 Komanso amakonda kukhala m’mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.+ 40 Iwo ndi amene amadyerera nyumba+ za akazi amasiye, ndipo mwachiphamaso amapereka mapemphero ataliatali. Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.”+

41 Ndiyeno anakhala pansi moyang’anana ndi moponyamo zopereka+ ndipo anali kuona mmene khamu la anthu linali kuponyera ndalama moponya zoperekamo. Anthu ambiri olemera anali kuponyamo makobidi ambiri.+ 42 Kenako panafika mkazi wamasiye wosauka ndipo anaponyamo timakobidi tiwiri tating’ono.+ 43 Choncho Yesu anaitana ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse amene aponya ndalama moponya zoperekamo.+ 44 Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.”+

13 Pamene Yesu anali kutuluka m’kachisi, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera!”+ 2 Koma Yesu ananena kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi?+ Pano sipadzatsala mwala+ uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”+

3 Tsopano atakhala pansi m’phiri la Maolivi, kachisi akuonekera bwino, Petulo,+ Yakobo, Yohane ndi Andireya anayamba kumufunsa kumbaliko kuti:+ 4 “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zili m’nthawi yake yamapeto n’chiyani?”+ 5 Choncho Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni.+ 6 Ambiri adzabwera m’dzina langa, ndi kunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+ 7 Komanso, mukadzamva phokoso la nkhondo ndi mbiri za nkhondo, musadzachite mantha. Zimenezi ziyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+

8 “Pakuti mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndiponso ufumu ndi ufumu wina.+ Kudzakhala zivomezi+ m’malo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.+ Zimenezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.+

9 “Koma inu khalani wochenjera. Anthu adzakuperekani kumakhoti aang’ono,+ ndipo adzakukwapulani m’masunagoge+ ndi kukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo.+ 10 Komanso, m’mitundu yonse uthenga wabwino+ uyenera ulalikidwe choyamba.+ 11 Koma pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani.+ Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zimenezo, pakuti wolankhula si inu, koma mzimu woyera.+ 12 Komanso, munthu adzapereka m’bale wake ku imfa, ndipo bambo adzapereka mwana wake,+ ndi ana adzaukira makolo awo ndi kuwaphetsa.+ 13 Ndipo anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ Koma amene adzapirire mpaka pa mapeto,+ ndiye amene adzapulumuke.+

14 “Koma mukadzaona chinthu chonyansa+ chosakaza+ chitaimirira pamene sichiyenera kuima (wowerenga adzazindikire),+ pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.+  15 Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike, kapena kulowa mkati kukatenga chilichonse m’nyumba mwakemo.+ 16 Ndipo munthu amene ali m’munda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya, kukatenga malaya ake akunja.+ 17 Tsoka kwa akazi apakati ndi oyamwitsa ana m’masiku amenewo!+ 18 Pitirizani kupemphera kuti zisadzachitike mu nyengo yachisanu.+ 19 Pakuti masiku amenewo adzakhala masiku a chisautso+ chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo, ndipo sichidzachitikanso.+ 20 Kunena zoona, Yehova akanapanda+ kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo,+ amene iye anawasankha,+ wafupikitsa masikuwo.+

21 “Komanso pa nthawiyo, munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’+ ‘Onani! Ali uko,’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 22 Pakuti kudzafika onamizira kukhala Khristu ndiponso aneneri onyenga,+ ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa+ kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse osankhidwawo.+ 23 Choncho inuyo khalani ochenjera.+ Ine ndakuuziranitu zinthu zonse.+

24 “Koma m’masiku amenewo, chisautso chimenecho chikadzatha, dzuwa lidzachita mdima, ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. 25 Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka.+ 26 Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemerero.+ 27 Ndiyeno adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa+ ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero ake a dziko lapansi kukafika kumalekezero a m’mlengalenga.+

28 “Tsopano phunzirani pa fanizo ili la mkuyu: Pamene nthambi yake yanthete yaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi.+ 29 Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti iye ali pafupi. Dziwani kuti ali pakhomo penipeni.+ 30 Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha konse, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.+ 31 Kumwamba+ ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu+ anga sadzachoka ayi.+

32 “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha.+ 33 Khalani maso, khalani tcheru,+ pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.+ 34 Zili ngati munthu amene anali kupita kutali kudziko lina,+ amene anasiya nyumba m’manja mwa akapolo ake, aliyense pa ntchito yake, ndi kulamula mlonda wa pachipata kuti azikhala maso. 35 Choncho khalani maso,+ pakuti simukudziwa nthawi yobwera mwininyumba. Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, atambala akulira, kapena m’mawa,*+ 36 kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona.+ 37 Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.”+

14 Tsopano kunangotsala masiku awiri kuti pasika+ ndi chikondwerero+ cha mikate yopanda chofufumitsa zichitike.+ Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anali kufunafuna njira yogwirira Yesu mochenjera ndi kumupha.+ 2 Iwo nthawi zonse anali kunena kuti: “Tisadzamugwire pa chikondwerero, mwina anthu angadzachite chipolowe.”+

3 Ndiyeno Yesu ali ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate+ uja, ali pa chakudya, kunafika mayi wina ali ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala la mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado weniweni, okwera mtengo kwambiri. Atatsegula botolo la alabasitala lija mochita kuswa, anayamba kuthira mafutawo m’mutu mwa Yesu.+ 4 Poona izi, ena anakhumudwa ndi kunena kuti: “N’chifukwa chiyani akuwononga chonchi mafuta onunkhirawa?+ 5 Pakuti mafuta onunkhirawa akanagulitsidwa ndalama zoposa madinari 300 n’kuzipereka kwa osauka!” Chotero iwo anakhumudwa kwambiri ndi mayiyo.+ 6 Koma Yesu anati: “Mulekeni. N’chifukwa chiyani mukum’vutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino.+ 7 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ ndipo nthawi iliyonse imene mwafuna mungathe kuwachitira zabwino. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+ 8 Mayiyu wachita zimene angathe. Iye wapakiratu thupi langa mafuta onunkhira kukonzekera kuikidwa kwanga m’manda.+ 9 Ndithu ndikukuuzani, Kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe m’dziko lonse,+ anthu azidzanenanso zimene mayiyu wachita kuti azidzam’kumbukira.”+

10 Kenako Yudasi Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anachoka ndi kupita kwa ansembe aakulu kuti akapereke Yesu kwa iwo.+ 11 Atamva zimenezo, iwo anasangalala ndi kumulonjeza kuti am’patsa ndalama zasiliva.+ Choncho iye anayamba kufunafuna mpata wabwino umene angamuperekere.+

12 Tsopano pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ pamene mwa mwambo anali kupereka nsembe nyama ya pasika, ophunzira ake+ anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tipite kuti kumene tikakukonzereni malo odyerako pasika?”+ 13 Pamenepo Yesu anatuma awiri mwa ophunzira akewo ndi kuwauza kuti: “Pitani mumzinda, ndipo mwamuna wina wosenza mtsuko wa madzi akakumana nanu.+ Mukam’tsatire ameneyo, 14 ndipo m’nyumba imene akalowe, mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi akufunsa kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti, mmene ine ndidyeremo pasika+ pamodzi ndi ophunzira anga?”’+ 15 Iye akakusonyezani chipinda chachikulu cham’mwamba, chokonzedwa bwino. Mukatikonzere pasika mmenemo.”+ 16 Choncho ophunzirawo anapita ndi kulowa mumzinda, ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Chotero anakonzekera pasika kumeneko.+

17 Chakumadzulo ndithu, Yesu anafika limodzi ndi ophunzira ake 12 aja.+ 18 Ndipo akudya chakudya patebulo, Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani, Mmodzi wa inu, amene akudya+ nane limodzi, andipereka.”+ 19 Pamenepo chisoni chinawagwira ndipo anayamba kumufunsa mmodzimmodzi kuti: “Kodi ndine kapena?”+ 20 Iye anati: “Ndi mmodzi wa inu 12, amene akusunsa nane m’mbale imodzi.+ 21 Zoona, Mwana wa munthu akuchokadi, monga Malemba amanenera za iye. Koma tsoka kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu! Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.”+

22 Pamene anali kudya, iye anatenga mkate ndi kupempha dalitso. Kenako anaunyemanyema ndi kuwapatsa, ndipo anati: “Tengani, mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 23 Kenako anatenga kapu ndi kuyamika, n’kuipereka kwa iwo, ndipo onse anamwa.+ 24 Ndiyeno anawauza kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi+ anga a pangano,’+ amene adzakhetsedwa+ chifukwa cha anthu ambiri.+ 25 Ndithu ndikukuuzani, sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa kufikira tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”+ 26 Potsirizira pake, atatha kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,+ anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.+

27 Tsopano Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa kundisiya ndekha, chifukwa Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa,+ ndipo nkhosa zidzabalalika.’+ 28 Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya+ inu musanafikeko.” 29 Ndiyeno Petulo anauza Yesu kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, koma ine ndekha sindidzatero.”+ 30 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza, iweyo lero, usiku womwe uno, tambala asanalire kawiri, undikana katatu.”+ 31 Koma iye ananena molimba mtima kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ndipo ena onse anayamba kunenanso chimodzimodzi.+

32 Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikukapemphera.”+ 33 Popita kumeneko anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane,+ ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika kwambiri mumtima mwake.+ 34 Ndiyeno anawauza kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho.+ Khalani pompano ndipo mukhalebe maso.”+ 35 Choncho atapita patsogolo pang’ono anadzigwetsa pansi ndipo anayamba kupemphera kuti ngati zikanatheka, asakumane ndi mayesero amenewa.+ 36 Kenako anati: “Abba,* Atate,+ zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+ 37 Tsopano anabwerera ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Simoni, zoona ukugona? Kodi unalibe mphamvu kuti ukanakhalabe maso ola limodzi?+ 38 Amuna inu, khalani maso ndipo muzipemphera,+ kuti musalowe m’mayesero. Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 39 Atatero anachokanso kupita kukapemphera, motchula mawu omwe aja.+ 40 Atabweranso anawapezanso akugona, pakuti zikope zawo zinali zitalemera ndi tulo, ndipo iwo anasowa chomuyankha.+ 41 Anabweranso kachitatu ndi kuwauza kuti: “Koma zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula! Basi! Nthawi yakwana!+ Taonani! Mwana wa munthu akuperekedwa m’manja mwa ochimwa.+ 42 Nyamukani, tiyeni tizipita.+ Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+

43 Nthawi yomweyo, mawu adakali m’kamwa, Yudasi, mmodzi wa ophunzira ake 12 aja, anafika limodzi ndi khamu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu, atanyamula malupanga ndi zibonga.+ 44 Apa n’kuti womupereka ameneyu atawapatsa chizindikiro chimene anagwirizana nawo, chakuti: “Amene ndim’psompsone ndi ameneyo. Mum’gwire ndi kupita naye osam’taya.”+ 45 Pamenepo Yudasi anayenda molunjika ndi kufika kwa iye. Kenako anati: “Rabi!” Ndipo anam’psompsona.+ 46 Choncho iwo anam’gwira ndi kum’manga.+ 47 Koma wina mwa amene anaimirira chapafupi anasolola lupanga lake ndi kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 48 Koma Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba?+ 49 Tsiku ndi tsiku ndinali nanu m’kachisi kuphunzitsa,+ koma simunandigwire. Komabe, izi zikuchitika kuti Malemba+ akwaniritsidwe.”+

50 Pamenepo ophunzira ake onse anathawa ndi kumusiya+ yekha.+ 51 Koma mnyamata wina amene anafunda nsalu yake yabwino popanda chovala china mkati, anayamba kumutsatira chapafupi ndithu. Anthuwo anayesa kumugwira,+ 52 koma iye anawasiyira m’manja nsalu yake ija, ndi kuthawa ali maliseche.*

53 Tsopano iwo anatengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo ansembe aakulu komanso akulu ndi alembi onse anasonkhana kumeneko.+ 54 Koma Petulo, anali kum’tsatira chapatali ndithu,+ mpaka anafika m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe. Kumeneko iye anakhala pansi pamodzi ndi antchito a m’nyumbamo, n’kumawotha moto walawilawi. 55 Pa nthawiyi ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* anali kufunafuna umboni kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha,+ koma sanali kuupeza.+ 56 Ndipo anthu ambiri anali kupereka umboni wonama kutsutsana naye,+ koma maumboni awowo anali kutsutsana.+ 57 Komanso, ena anali kuimirira ndi kupereka umboni womunamizira kuti: 58 “Ife tinamva iyeyu akunena kuti, ‘Ine ndidzagwetsa kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja, ndipo m’masiku atatu okha ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja.’”+ 59 Komabe ngakhale pa mfundo zimenezi, umboni wawo sunali wogwirizana.

60 Potsirizira pake, mkulu wa ansembe anaimirira pakati pawo ndi kufunsa Yesu kuti: “Sukuyankha chilichonse? Kodi n’zoona zimene awa akukunenezazi?”+ 61 Koma iye anangokhala chete osanena chilichonse.+ Apanso mkulu wa ansembe anayamba kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsidwayo?”+ 62 Pamenepo Yesu anati: “Inde ndinedi, ndipo anthu inu mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera ndi mitambo yakumwamba.”+ 63 Tsopano mkulu wa ansembe atamva zimenezi anang’amba malaya ake amkati+ ndi kunena kuti: “Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa?+ 64 Mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu.+ Mukuona bwanji pamenepa?” Onse anati ayenera kuphedwa basi. 65 Pamenepo ena anayamba kumulavulira,+ kumuphimba nkhope ndi kumukhoma nkhonya. Iwo anali kunena kuti: “Losera!” Atamuwomba mbama, asilikali a pakhoti anamutenga.+

66 Tsopano pamene Petulo anali m’munsi, m’bwalo lamkati, mmodzi wa atsikana antchito a mkulu wa ansembe anabwera.+ 67 Ataona Petulo akuwotha moto, anamuyang’anitsitsa ndi kunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu, Mnazareti uja.”+ 68 Koma iye anakana kuti: “Ngakhale kumudziwa, sindikumudziwa ameneyo, ndipo sindikumvetsa kuti ukunena chiyani.” Atatero anatuluka panja ndi kupita kukachipinda ka kuchipata.+ 69 Kumenekonso mtsikana wantchito atamuona, anayamba kuuzanso amene anali ataimirira chapafupi kuti: “Bambo awanso ali m’gulu la ophunzira ake.”+ 70 Apanso anakana. Patapitanso kanthawi pang’ono, amene anali ataimirira chapafupi anayamba kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake. Ndipo ndiwenso Mgalileya.”+ 71 Koma iye anayamba kudzitemberera ndi kulumbira kuti:+ “Munthu amene mukunenayu ine sindikumudziwa ayi.”+ 72 Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri.+ Pamenepo Petulo anakumbukira mawu amene Yesu anamuuza aja, akuti: “Tambala asanalire kawiri, udzandikana katatu.”+ Ndipo anamva chisoni ndi kuyamba kulira.+

15 Mwamsanga m’bandakucha, ansembe aakulu, akulu ndi alembi, kutanthauza Khoti lonse Lalikulu la Ayuda,* anasonkhana pamodzi ndi kugwirizana chimodzi.+ Kenako anamanga Yesu ndi kukam’pereka kwa Pilato.+ 2 Choncho Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu+ ya Ayuda?” Iye anayankha kuti: “Mukunena nokha.”+ 3 Koma ansembe aakulu anapitiriza kumuneneza zinthu zambiri.+ 4 Tsopano Pilato anamufunsanso kuti: “Kodi ukusowa choyankha?+ Taona kuchuluka kwa milandu imene akukuneneza.”+ 5 Koma Yesu sanayankhenso chilichonse, moti Pilato anadabwa kwambiri.+

6 Pa chikondwerero chilichonse, Pilato anali kumasulira anthu mkaidi mmodzi amene iwo apempha.+ 7 Pa nthawiyo panali wina wotchedwa Baraba, amene anali m’ndende limodzi ndi oukira boma. Iwo anapha munthu pa kuukira kwawoko.+ 8 Choncho khamu la anthu linafika ndi kuyamba kupempha malinga ndi zimene iye anali kuwachitira nthawi zonse. 9 Pilato anawafunsa kuti: “Kodi mukufuna ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?”+ 10 Pakuti iye anadziwa kuti ansembe aakulu anamupereka chifukwa cha kaduka.+ 11 Koma ansembe aakulu analimbikitsa anthu kupempha kuti awamasulire Baraba.+ 12 Poyankha, Pilato anawafunsa kuti: “Nanga uyu amene mumati ndi mfumu+ ya Ayuda, ndichite naye chiyani?”+ 13 Pamenepo iwo anafuula kuti: “M’pachikeni!”+ 14 Koma Pilato anapitiriza kuwafunsa kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma atatero m’pamene anawonjezera kufuula kuti: “M’pachikeni!”+ 15 Pamenepo Pilato, pofuna kukwaniritsa zofuna za anthuwo,+ anawamasulira Baraba. Ndipo atalamula kuti Yesu amukwapule, anamupereka kuti akamupachike.+

16 Tsopano asilikali anamutenga ndi kupita naye m’bwalo lamkati kunyumba ya bwanamkubwa. Kumeneko anasonkhanitsa khamu lonse la asilikali.+ 17 Ndiyeno anamuveka chovala cha maonekedwe ofiirira ndi kuluka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka.+ 18 Tsopano anayamba kum’lonjera kuti: “Mtendere ukhale nanu,+ inu Mfumu ya Ayuda!” 19 Komanso anali kum’menya m’mutu ndi bango ndi kumulavulira, ndipo anali kugwada ndi kumuweramira.+ 20 Atamaliza kumuchitira zachipongwezo, anamuvula chovala chofiirira chija ndi kumuveka malaya ake akunja. Atatero anatuluka naye kupita kokamupachika.+ 21 Komanso, iwo anasenzetsa mtengo wake wozunzikirapo* munthu wongodutsa, dzina lake Simoni wa ku Kurene, amene anali kuchokera kudera la kumidzi, bambo wa Alekizanda ndi Rufu.+

22 Choncho anafika naye kumalo otchedwa Gologota. Liwuli akalimasulira, limatanthauza Malo a Chibade.+ 23 Kumeneko anayesa kum’patsa vinyo wosakaniza ndi mule,+ koma iye anakana.+ 24 Pamenepo anamupachika pamtengo ndi kugawana malaya ake akunja+ mwa kuchita maere pamalayawo, kuti aone chimene munthu aliyense angatenge.+ 25 Tsopano nthawi ili cha m’ma 9 koloko m’mawa,*+ iwo anam’pachika. 26 Ndiyeno mawu osonyeza mlandu wake+ anawalemba pamwamba pake kuti: “Mfumu ya Ayuda.”+ 27 Komanso iwo anapachika achifwamba awiri limodzi ndi iye. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja, wina kumanzere kwake.+ 28* —— 29 Anthu amene anali kudutsa pamenepo anali kumulankhula monyoza.+ Anali kupukusa mitu yawo n’kumanena kuti: “Iwe wogwetsa kachisi ndi kum’manga m’masiku atatu,+ 30 dzipulumutse. Tsika pamtengo wozunzikirapowo.”+ 31 Chimodzimodzinso ansembe aakulu. Nawonso anali kumuchita chipongwe limodzi ndi alembi. Iwo anali kunena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikum’kanika!+ 32 Tsopanotu Khristu, Mfumu ya Isiraeli, itsike pamtengo wozunzikirapowo, kuti ife tione ndi kukhulupirira.”+ Ngakhale amene anapachikidwa naye limodziwo analinso kumunyoza.+

33 Nthawi itafika cha m’ma 12 koloko masana,* kunagwa mdima m’dziko lonselo mpaka 3 koloko masana.*+ 34 Ndipo cha m’ma 3 kolokomo, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+ 35 Tsopano ena mwa anthu amene anaimirira chapafupi, atamva zimenezo, anayamba kunena kuti: “Tamverani! Akuitana Eliya.”+  36 Koma wina anathamanga kukaviika chinkhupule m’vinyo wowawasa, kenako anachiika kubango ndi kum’patsa kuti amwe,+ ndikunena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”+  37 Ndiyeno Yesu anafuula mokweza mawu, ndipo anatsirizika.+ 38 Pamenepo nsalu yotchinga+ ya m’nyumba yopatulika inang’ambika pakati, kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ 39 Tsopano, kapitawo wa asilikali amene anaimirira chapafupi moyang’ana Yesu, ataona zimene zinachitika pa nthawi imene anatsirizika, ananena kuti: “Ndithudi munthu uyu analidi Mwana wa Mulungu.”+

40 Panali amayi amene anali kuonerera chapatali ndithu,+ ena mwa iwo anali Mariya Mmagadala, Mariya mayi wa Yakobo Wamng’ono ndi Yose, komanso Salome,+ 41 amene anali kuyenda naye limodzi+ ndi kumutumikira pamene anali ku Galileya. Panalinso amayi ena ambiri amene anabwera naye limodzi kuchokera ku Yerusalemu.+

42 Tsopano madzulo, popeza linali Tsiku Lokonzekera, kapena kuti tsiku loti m’mawa mwake ndi sabata, 43 Yosefe wa ku Arimateya, munthu wodziwika wa m’Bungwe Lalikulu la Ayuda, amenenso anali kuyembekezera ufumu wa Mulungu,+ anapita kwa Pilato molimba mtima kukapempha mtembo+ wa Yesu. 44 Koma Pilato anali kukayikira ngati anali atamwalira kale, choncho anaitanitsa kapitawo wa asilikali ndi kumufunsa ngatidi iye wamwalira kale. 45 Atatsimikizira kuchokera kwa kapitawo wa asilikaliyo, analola kuti Yosefe akatenge mtembowo.+ 46 Ndiyeno Yosefe anagula nsalu yabwino kwambiri ndi kumutsitsa. Atatero anamukulunga ndi nsalu yabwino kwambiri ija ndi kumuika+ m’manda+ amene anawasema m’thanthwe. Anagubuduza chimwala ndi kutseka pakhomo la manda achikumbutsowo.+ 47 Koma Mariya Mmagadala ndi Mariya mayi wa Yose, anali kuyang’anitsitsa pamene anaikidwapo.+

16 Choncho tsiku la sabata+ litapita, Mariya Mmagadala,+ Mariya mayi wa Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhira kuti akapake thupi la Yesu.+ 2 M’mawa kwambiri tsiku loyamba+ la mlunguwo, iwo anafika kumanda achikumbutsowo, dzuwa litatuluka.+ 3 Iwo anali kufunsana kuti: “Nanga ndani amene akatigubuduzire chimwala chija pakhomo la manda achikumbutso?” 4 Koma atayang’anitsitsa, anaona kuti mwalawo wagubuduzidwa kale ngakhale kuti unali waukulu kwambiri.+ 5 Atalowa m’manda achikumbutsowo, anaona mnyamata atakhala pansi kudzanja lamanja, atavala mkanjo woyera, ndipo iwo anadabwa kwambiri.+ 6 Iye anawauza kuti: “Musadabwe choncho. Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu Mnazareti, amene anapachikidwa.+ Iyetu wauka kwa akufa,+ salinso muno ayi. Taonani! Si apa pamene anamugoneka!+ 7 Inuyo pitani, mukauze ophunzira ake komanso Petulo kuti, ‘Watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona, monga anakuuzirani.’”+ 8 Tsopano iwo atatuluka, m’manda achikumbutsowo anayamba kuthawa, pakuti anali kunjenjemera ndi kunthunthumira kwambiri. Ndipo sanaulule kanthu kwa aliyense, chifukwa anagwidwa ndi mantha.+

MAWU OMALIZA AAFUPI

Mipukutu ndi Mabaibulo ena amene analembedwa pambuyo pake ali ndi mawu omaliza aafupi awa pambuyo pa Maliko 16:8:

Koma zinthu zonse zimene analamula, iwo anazifotokoza mwachidule kwa amene anali pafupi ndi Petulo. Komanso izi zitatha, Yesu mwiniyo anatumiza uthenga woyera ndi wosawonongeka wa chipulumutso chosatha kudzera mwa ophunzira, kuchokera kum’mawa mpaka kumadzulo.

MAWU OMALIZA AATALI

Mipukutu ina yakale (Codex Alexandrinus, Codex Ephraemi, Codex Bezae) ndi Mabaibulo ena (Latin Vulgate, Curetonian Syriac, Syriac Peshitta) anawonjezera mawu omaliza aatali otsatirawa, koma mawuwa anawachotsamo m’mipukutu yotchedwa Codex Sinaiticus, Codex Vaticanus, the Sinaitic Syriac codex, komanso mu Armenian Version:

9 Atauka m’mawa tsiku loyamba la mlungu, anaonekera choyamba kwa Mariya Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7. 10 Mayiyu anapita ndi kukauza amene anali kukhala ndi Yesu, pakuti anali achisoni ndipo anali kulira. 11 Koma iwo, pamene anamva kuti ali moyo ndi kuti iye wamuona, sanakhulupirire. 12 Komanso, izi zitachitika anaonekera mwamtundu wina kwa awiri a iwo pamene anali kuyenda nawo limodzi popita kumidzi. 13 Pamenepo iwo anabwerera ndi kukauza enawo. Ndipo nawonso sanakhulupirire zimenezo. 14 Koma pambuyo pake anaonekera kwa ophunzira 11 aja pamene anali kudya chakudya patebulo. Pamenepo iye anawadzudzula chifukwa chosowa chikhulupiriro ndi kuuma mitima kwawo, pakuti iwo sanakhulupirire anthu amene anamuona atauka kwa akufa. 15 Iye anawauza kuti: “Pitani m’dziko lonse ndi kukalalikira uthenga wabwino ku cholengedwa chilichonse. 16 Amene adzakhulupirira ndi kubatizidwa adzapulumuka, koma amene sadzakhulupirira adzaweruzidwa. 17 Komanso, okhulupirira adzachita zizindikiro izi: M’dzina langa adzatulutsa ziwanda, ndi kulankhula m’malilime. 18 Adzanyamula njoka ndi manja awo, ndipo akadzamwa chilichonse chakupha sichidzawavulaza ngakhale pang’ono. Adzaika manja awo pa anthu odwala, ndipo adzachira.”

19 Choncho Ambuye Yesu atatsiriza kulankhula nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndi kukakhala kudzanja lamanja la Mulungu. 20 Pamenepo iwo anachoka ndi kupita kukalalikira kwina kulikonse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito limodzi ndi kutsimikizira uthengawo mwa zizindikiro zimene anali kuchita.

Mawu amene ali m’mikutiramawu Maliko anawagwira pa Mki 3:1.

Onani Zakumapeto 2.

M’Baibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete, komanso nyanja ya Tiberiyo.

Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”

Kapena kuti “tsindwi.”

Dzina lakuti “Kananiya” likutanthauza munthu wachangu.

Limeneli ndi dzina lina la Satana.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakang’ono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita anayi ndipo kamachita nthambi.

Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.

Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:25.

Onani mawu a m’munsi pa Mt 15:2.

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.

Onani Zakumapeto 7.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto 9.

Onani Zakumapeto 9.

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.

Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.

Onani Zakumapeto 2.

Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:25.

Mawu achiaramu otanthauza “ababa,” kapena, “Bambo anga!”

Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “ali maliseche” angatanthauze kuti “atavala zovala zamkati zokha,” osati ali mbulanda kapena asanavale chilichonse.

Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”

Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”

Onani Zakumapeto 9.

Mawu ake enieni, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.

Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.

Mawu ake enieni, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena