Luka
1 Ambiri anayesetsa kulemba nkhani yofotokoza zochitika zenizeni+ zimene ife tonse timazikhulupirira. 2 Iwo analemba ndendende mmene anatiuzira anthu amene anakhala mboni zoona ndi maso+ ndi atumiki a uthengawo+ kuchokera pa chiyambi.+ 3 Inenso, popeza kuti ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi, ndafunitsitsa kuti ndikulembereni mwatsatanetsatane,+ inu wolemekezeka+ koposa, a Teofilo.+ 4 Ndachita izi kuti mudziwe bwinobwino kuti zinthu zimene anakuphunzitsani ndi mawu apakamwa n’zodalirika.+
5 M’masiku a Herode,*+ mfumu ya Yudeya, kunali wansembe wina wotchedwa Zekariya wa m’gulu la ansembe lotchedwa Abiya.+ Iyeyu anali ndi mkazi wochokera mwa ana aakazi a Aroni,+ dzina lake Elizabeti. 6 Onse awiriwo anali olungama+ pamaso pa Mulungu chifukwa choyenda mokhulupirika,+ mogwirizana ndi malamulo onse+ komanso zofunika za m’chilamulo+ cha Yehova.+ 7 Koma iwo analibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabereka,+ ndipo onse awiri anali okalamba.
8 Tsopano pamene Zekariya anali kugwira ntchito monga wansembe pamaso pa Mulungu, kuimira gawo lake,+ 9 malinga ndi mwambo wa ansembe, inali nthawi yake yakuti azilowa m’nyumba yopatulika ya Yehova,+ n’kupereka nsembe zofukiza.+ 10 Khamu lonse la anthu linali kupemphera panja, pa ola lopereka nsembe zofukizalo.+ 11 Mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye, ataimirira kudzanja lamanja la guwa lansembe zofukiza.+ 12 Tsopano Zekariya anavutika mumtima ataona zimenezo, ndipo anagwidwa ndi mantha.+ 13 Koma mngeloyo anamuuza kuti: “Usachite mantha Zekariya, chifukwa pembedzero lako lamveka ndithu.+ Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera mwana wamwamuna, ndipo udzamutche Yohane.+ 14 Udzakondwa ndi kusangalala kwambiri, ndipo ambiri adzasangalala+ ndi kubadwa kwake 15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova.+ Koma asadzamwe vinyo ngakhale pang’ono+ kapena chakumwa chaukali chilichonse. Ndipo adzadzazidwa ndi mzimu woyera kuyambira ali m’mimba mwa mayi ake.+ 16 Iye adzatembenuza ana ambiri a Isiraeli kuti abwerere kwa Yehova+ Mulungu wawo. 17 Komanso, adzatsogola monga kalambulabwalo wa Mulungu ali ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.+ Iye adzatembenuza mitima+ ya abambo kuti ikhale ngati ya ana, ndipo osamvera adzawatembenuzira ku nzeru yeniyeni ya anthu olungama. Adzachita izi kuti asonkhanitsire Yehova+ anthu okonzedwa.”+
18 Ndiyeno Zekariya anafunsa mngeloyo kuti: “Nditsimikiza bwanji zimenezi? Inetu ndine wokalamba,+ mkazi wanganso zaka zake n’zambiri.” 19 Poyankha mngeloyo anamuuza kuti: “Ine ndine Gabirieli,+ amene ndimaima pamaso pa Mulungu, ndipo wandituma kudzalankhula+ nawe ndi kudzalengeza uthenga wabwino wa zinthu izi kwa iwe. 20 Imva tsopano! Udzakhala chete,+ osatha kulankhula mpaka tsiku limene zimenezi zidzachitike. Izi zidzachitika chifukwa sunakhulupirire mawu anga amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoikidwiratu.” 21 Pa nthawiyi n’kuti anthu akuyembekezerabe Zekariya,+ ndipo anayamba kudabwa ndi kuchedwa kwake m’nyumba yopatulikayo. 22 Koma pamene anatuluka sanathenso kulankhula nawo. Pamenepo iwo anazindikira kuti waona masomphenya+ a chinachake m’nyumba yopatulikayo. Choncho anayamba kulankhula nawo ndi manja okhaokha, osathanso kutulutsa mawu. 23 Tsopano masiku ake otumikira atatha,+ anapita kwawo.
24 Masiku amenewa atadutsa, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati,+ ndipo anabindikira miyezi isanu. Iye anali kunena kuti: 25 “Izitu n’zimene Yehova wandichitira masiku ano pamene wandicheukira kuti andichotsere chitonzo pamaso pa anthu.”+
26 M’mwezi wake wa 6, Mulungu anatumiza mngelo Gabirieli+ kumzinda wina wa Galileya, wotchedwa Nazareti. 27 Anamutumiza kwa namwali amene mwamuna wina wotchedwa Yosefe, wa m’nyumba ya Davide, anamulonjeza kuti adzamukwatira. Namwali+ ameneyu dzina lake anali Mariya.+ 28 Mngelo uja atafika kwa namwaliyu anati: “Mtendere ukhale nawe,+ iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova+ ali nawe.”+ 29 Koma mawu amenewa anam’dabwitsa kwambiri, moti anayamba kusinkhasinkha za moni wamtundu woterewu. 30 Pamenepo mngeloyo anamuuza kuti: “Usaope Mariya, pakuti Mulungu wakukomera mtima.+ 31 Tsopano mvetsera! Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna.+ Udzam’patse dzina lakuti Yesu.+ 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.+ Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu+ wa Davide atate wake.+ 33 Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha konse.”+
34 Koma Mariya anafunsa mngeloyo kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, pakuti sindinagonepo+ ndi mwamuna?” 35 Poyankha mngeloyo anauza Mariya kuti: “Mzimu woyera+ udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera,+ Mwana wa Mulungu.+ 36 Ndipotu m’bale wako Elizabeti, amene anthu amamunena kuti mkazi wosabereka,+ nayenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake, ndipo uno ndi mwezi wa 6. 37 Izi zachitika chifukwa zimene Mulungu wanena, sizilephereka.”+ 38 Ndiyeno Mariya anati: “Ndinetu kapolo wa Yehova!+ Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” Pamenepo mngeloyo anamusiya.
39 Choncho Mariya ananyamuka m’masiku amenewo n’kupita mofulumira kudera lamapiri, kumzinda wina m’dziko la fuko la Yuda. 40 Kumeneko analowa m’nyumba ya Zekariya ndi kupereka moni kwa Elizabeti. 41 Tsopano Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali m’mimba mwakemo linadumpha. Ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera. 42 Choncho anafuula ndi mawu amphamvu, kuti: “Ndiwe wodalitsidwa mwa akazi onse. N’chodalitsidwanso+ chipatso cha mimba yako! 43 Koma zatheka bwanji kuti dalitso limeneli lindigwere? Zatheka bwanji kuti mayi wa Mbuye wanga+ abwere kwa ine? 44 Waona nanga! Pamenetu mawu a moni wako alowa m’makutu mwangamu, ndithu khanda ladumpha mosangalala kwambiri m’mimba mwangamu.+ 45 Ndipotu ndiwe wodala pakuti unakhulupirira, chifukwa zonse zimene unauzidwa zochokera kwa Yehova+ zidzachitika.”+
46 Pamenepo Mariya anati: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova.+ 47 Ndipo mzimu wanga sungaleke kusefukira+ ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga.+ 48 Chifukwa waona malo otsika a kapolo wake.+ Ndipo taonani! kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditcha wodala.+ 49 Chifukwa Wamphamvuyo wandichitira zazikulu, ndipo dzina lake ndi loyera.+ 50 Chifundo chake chakhala pa amene amamuopa ku mibadwomibadwo.+ 51 Wachita zamphamvu ndi dzanja lake,+ wabalalitsira kutali odzikweza m’zolinga za mitima yawo.+ 52 Watsitsa anthu amphamvu+ zawo pamipando yachifumu, ndipo wakweza anthu wamba.+ 53 Wakhutitsa anthu anjala ndi zinthu zabwino,+ amene anali ndi chuma wawapitikitsa chimanjamanja.+ 54 Iye wathandiza mtumiki wake Isiraeli.+ Wachita zimenezi posonyeza kuti akukumbukira lonjezo lake lakuti adzasonyeza chifundo kwamuyaya,+ 55 monga momwe anauzira makolo athu akale, Abulahamu ndi mbewu yake.”+ 56 Choncho Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu, kenako anabwerera kwawo.
57 Tsopano nthawi inakwana yakuti Elizabeti achire, ndipo anabereka mwana wamwamuna. 58 Anthu oyandikana naye ndi abale ake anamva kuti Yehova anam’chitira chifundo chachikulu,+ ndipo anayamba kukondwera+ naye pamodzi. 59 Pa tsiku la 8, iwo anabwera kudzachita mdulidwe wa mwanayo,+ komanso anafuna kum’patsa dzina la bambo ake, lakuti Zekariya. 60 Koma mayi ake anayankha kuti: “Limenelo iyayi! Dzina lake akhala Yohane.” 61 Pamenepo iwo anamuuza kuti: “Palibe wachibale wako aliyense wotchedwa ndi dzina limenelo.” 62 Ndiyeno anafunsa bambo wake, mwa kulankhula ndi manja, za dzina limene akufuna kuti am’tchule mwanayo. 63 Choncho iye anapempha cholembapo chathabwa ndipo analemba kuti: “Dzina lake ndi Yohane.”+ Pamenepo onse anadabwa. 64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatseguka,+ lilime lake linamasuka, ndipo anayamba kulankhula ndi kutamanda Mulungu. 65 Pamenepo onse okhala moyandikana nawo anagwidwa mantha. Ndipo nkhani imeneyi inali m’kamwam’kamwa m’madera onse a kumapiri a Yudeya. 66 Mwakuti onse amene anamva anazisunga m’mitima mwawo ndi kuzisinkhasinkha.+ Iwo anali kunena kuti: “Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani kwenikweni?” Pakuti dzanja+ la Yehova linalidi pa iye.
67 Pamenepo bambo ake Zekariya anadzazidwa ndi mzimu woyera,+ ndipo ananenera,+ kuti: 68 “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ chifukwa wacheukira anthu ake+ ndi kuwapatsa chipulumutso.+ 69 Iye watikwezera ife nyanga*+ yachipulumutso m’nyumba ya mtumiki wake Davide, 70 monga mmene iye ananenera kudzera pakamwa pa aneneri ake oyera akale,+ 71 za kutipulumutsa kwa adani athu ndiponso m’manja mwa onse odana nafe.+ 72 Kuchitira chifundo makolo athu akale ndi kukumbukira pangano lake loyera,+ 73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu lakale Abulahamu,+ 74 kuti pambuyo pakuti tapulumutsidwa m’manja mwa adani,+ atipatse mwayi wochita utumiki wopatulika kwa iye+ mopanda mantha, 75 mokhulupirika ndi mwachilungamo pamaso pake masiku athu onse.+ 76 Koma kunena za iwe, mwanawe, udzatchedwa mneneri wa Wam’mwambamwamba, pakuti udzatsogola pamaso pa Yehova kuti ukakonzeretu njira zake.+ 77 Kukadziwitsa anthu ake za chipulumutso pokhululukidwa machimo awo,+ 78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu. Ndi chifundo chimenechi, kuwala kwa m’mawa+ kudzatifikira kuchokera kumwamba,+ 79 ndipo kudzaunikira amene akhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa,+ ndi kutsogolera bwinobwino mapazi athu panjira yamtendere.”
80 Choncho mwana uja anakulirakulira+ ndipo anali kulimba mwauzimu. Iye anali kukhala m’zipululu mpaka tsiku lakuti adzionetsere poyera kwa Isiraeli.
2 Tsopano m’masiku amenewo, Kaisara Augusito analamula+ kuti anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula. 2 Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya. 3 Anthu onse anapita kukalembetsa,+ aliyense kumzinda wakwawo. 4 Yosefe nayenso anachoka ku Galileya, mumzinda wa Nazareti, n’kupita ku Yudeya, kumzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu,+ chifukwa anali wa m’banja ndi m’fuko la Davide.+ 5 Anapita kukalembetsa limodzi ndi Mariya,+ amene anamanga naye banja malinga ndi pangano.+ Pa nthawiyi n’kuti Mariya tsopano ali wotopa ndi pakati.+ 6 Ali kumeneko, masiku oti achire anakwana. 7 Ndipo anabereka mwana wake woyamba wamwamuna.+ Anamukulunga ndi nsalu n’kumugoneka modyeramo ziweto,+ chifukwa anasowa malo m’nyumba ya alendo.
8 M’dzikomo munalinso abusa amene anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse mosinthana maulonda. 9 Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova+ anaima chapafupi ndi iwo, ndipo ulemerero wa Yehova+ unawawalira ponsepo, mwakuti anachita mantha kwambiri. 10 Koma mngeloyo anawauza kuti: “Musaope! Ine ndabwera kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu chimene anthu onse adzakhala nacho.+ 11 Chifukwa lero wakubadwirani Mpulumutsi,+ amene ndi Khristu Ambuye,+ mumzinda wa Davide.+ 12 Ndikukupatsani chizindikiro ichi: Mukapeza mwana wakhanda wokutidwa m’nsalu, atagona modyeramo ziweto.” 13 Mwadzidzidzi, panaoneka khamu lalikulu lakumwamba+ pamodzi ndi mngeloyo, likutamanda Mulungu+ kuti: 14 “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba,+ ndipo pansi pano mtendere+ pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”+
15 Choncho angelowo atawachokera kubwerera kumwamba, abusawo anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu tikaone zimene zachitikazo, zimene Yehova+ watidziwitsa.” 16 Pamenepo anapita mwachangu ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atagona modyeramo ziweto. 17 Ataona khandalo, anafotokoza zimene anauzidwa zokhudza mwana ameneyu. 18 Onse amene anamva anadabwa ndi zimene abusawo anali kuwauza. 19 Koma Mariya anasunga mawu onsewa ndi kuganizira tanthauzo la zimenezi mumtima mwake.+ 20 Ndiyeno abusa aja anabwerera, akulemekeza ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anamva ndi kuziona, ndendende mmene anawauzira muja.
21 Tsopano masiku 8+ atakwanira kuti achite mdulidwe+ wa mwanayo, anamupatsanso dzina lakuti Yesu.+ Dzina limeneli ndi limene mngelo uja anatchula m’mbuyomo, Mariya asanakhale ndi pakati.+
22 Komanso, masiku akuti iwo ayeretsedwe+ malinga ndi chilamulo cha Mose atakwanira, anapita naye ku Yerusalemu kukam’pereka kwa Yehova. 23 Izi zinali zogwirizana ndi zimene Malemba amanena m’chilamulo cha Yehova kuti: “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa adzakhala woyera kwa Yehova.”*+ 24 Kumeneko iwo anapereka nsembe malinga ndi zimene chilamulo cha Yehova chimanena kuti: “Njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.”+
25 Ndiyeno mu Yerusalemu munali munthu wina dzina lake Simiyoni. Mwamuna ameneyu anali wolungama ndi woopa Mulungu. Anali kuyembekezera nthawi imene Mulungu adzatonthoze Isiraeli,+ ndipo mzimu woyera unali pa iye. 26 Komanso Mulungu anamuululira mwa mzimu woyera kuti sadzafa asanaone Khristu+ wa Yehova. 27 Tsopano motsogoleredwa ndi mzimu,+ anabwera kukachisi. Ndipo pamene makolo a mwanayo, Yesu, anamubweretsa kudzamuchitira mwambo wa chilamulo,+ 28 iye analandira mwanayo m’manja mwake ndi kutamanda Mulungu, kuti: 29 “Tsopano, Ambuye Wamkulu Koposa, mukulola kapolo wanu kupita mu mtendere+ malinga ndi zimene inu munanena. 30 Chifukwa maso anga aona njira yanu yopulumutsira+ 31 imene mwakonzeratu pamaso pa mitundu yonse ya anthu.+ 32 Maso anga aona kuwala+ kochotsa nsalu yophimba+ mitundu ya anthu+ ndi ulemerero wa anthu anu Aisiraeli.” 33 Bambo ake ndi mayi ake anali kungodabwa ndi zimene Simiyoni anali kunena zokhudza mwanayo. 34 Komanso, Simiyoni anadalitsa makolowo, ndipo anauza Mariya, mayi a mwanayo kuti: “Tamverani! Uyu waikidwa kuti ambiri agwe,+ ndiponso kuti ambiri adzukenso mu Isiraeli,+ ndi kuti akhale chizindikiro chimene anthu adzachitsutse+ 35 kuti zimene anthu ambiri akuganiza mumtima mwawo zionekere poyera.+ Koma iwe lupanga lalitali lidzalasa moyo wako.”+
36 Kunalinso Anna mneneri wamkazi, mwana wa Fanueli, wa fuko la Aseri. Mayi ameneyu anali wachikulire kwambiri, ndipo anakhala ndi mwamuna wake zaka 7 zokha kuchokera pa unamwali wake. 37 Tsopano anali mkazi wamasiye,+ ndipo anali ndi zaka 84 koma sanali kusowa pakachisi. Anali kuchita utumiki wopatulika usana ndi usiku,+ anali kusala kudya ndi kupereka mapembedzero. 38 Mu ola limenelo, iye anafika pafupi ndi kuyamba kuyamika Mulungu. Komanso analankhula za mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.+
39 Choncho, atachita zonse mogwirizana ndi chilamulo+ cha Yehova, anabwerera ku Galileya, kumzinda wawo wa Nazareti.+ 40 Ndipo mwanayo anali kukulirakulira ndi kukhala wamphamvu.+ Nzeru zake zinali kuchuluka ndipo Mulungu anapitiriza kukondwera naye.+
41 Tsopano chaka ndi chaka makolo ake anali kukonda kupita ku Yerusalemu,+ ku chikondwerero cha pasika. 42 Choncho pamene anali ndi zaka 12, iwo anapita naye kumeneko malinga ndi mwambo+ wa chikondwererocho, 43 ndipo anakhala kumeneko mpaka tsiku lomaliza. Koma pamene anali kubwerera, mnyamatayo Yesu anatsalira ku Yerusalemu, ndipo makolo ake sanadziwe zimenezo. 44 Poganiza kuti iye anali nawo m’gulu la anthu apaulendowo, anayenda ulendo wa tsiku lathunthu.+ Kenako anayamba kumufunafuna mwa achibale ndi anzawo. 45 Koma atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anamufufuza pena paliponse. 46 Tsopano patapita masiku atatu, anamupeza ali m’kachisi,+ atakhala pakati pa aphunzitsi. Anali kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47 Koma onse amene anali kumumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.+ 48 Makolo akewo atamuona anadabwa kwambiri, ndipo mayi ake anamufunsa kuti: “Mwanawe, n’chifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Ine ndi bambo akowa tinada nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna.” 49 Koma iye anawayankha kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simunadziwe kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?”+ 50 Koma iwo sanamvetse zimene anali kuwauzazo.+
51 Pamenepo ananyamuka nawo limodzi kubwerera ku Nazareti, ndipo anapitiriza kuwamvera.+ Apanso mayi akewo anasunga mosamala kwambiri mawu onsewa mumtima mwawo.+ 52 Koma Yesu anali kukulabe m’nzeru+ ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.+
3 M’chaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode*+ anali wolamulira chigawo cha Galileya. Filipo m’bale wake anali wolamulira chigawo cha madera a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali wolamulira chigawo cha Abilene. 2 M’masiku amenewo Anasi anali wansembe wamkulu ndipo Kayafa+ anali mkulu wa ansembe. Pa nthawiyo mawu a Mulungu anafika kwa Yohane+ mwana wa Zekariya m’chipululu.+
3 Choncho iye anabwera m’midzi yonse yapafupi ndi Yorodano. Anali kulalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ 4 Anali kuchita zimenezi monga mmene analembera m’buku la mawu a Yesaya mneneri kuti: “Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti, ‘Konzani njira ya Yehova anthu inu! Wongolani misewu yake.+ 5 Dzenje lililonse likwiriridwe, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zisalazidwe. Njira zokhotakhota zikhale zowongoka ndipo malo okumbikakumbika akhale osalala bwino.+ 6 Anthu onse adzaona njira ya Mulungu yopulumutsira.’”+
7 Pamenepo anayamba kuuza khamu la anthu obwera kwa iye kudzabatizidwa kuti: “Ana a njoka inu,+ ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+ 8 Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kuti mwalapa.+ Ndipo musayambe kunena kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’ Pakuti ndikukuuzani kuti Mulungu ali ndi mphamvu yokhoza kuutsira Abulahamu ana kuchokera ku miyala iyi. 9 Ndithudi, nkhwangwa yaikidwa kale pamizu ya mitengo. Chotero mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa ndi kuponyedwa pamoto.”+
10 Ndiyeno khamu la anthu linali kumufunsa kuti: “Nanga tichite chiyani?”+ 11 Poyankha iye anali kuwauza kuti: “Munthu amene ali ndi malaya awiri amkati agawireko munthu amene alibiretu. Amenenso ali ndi chakudya achite chimodzimodzi.”+ 12 Okhometsa msonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa, ndipo anali kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, tichite chiyani?”+ 13 Iye anali kuwauza kuti: “Musamalipiritse anthu zochuluka kuposa msonkho woikidwa.”+ 14 Komanso, asilikali anali kumufunsa kuti: “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anali kuwauza kuti: “Musamavutitse anthu kapena kunamizira+ aliyense, koma muzikhutira ndi zimene mumalandira.”+
15 Tsopano pamene anthu anali kuyembekezera Khristu, ndipo onse anali kuganiza m’mitima yawo za Yohane kuti: “Kodi Khristu uja si ameneyu?”+ 16 Yohane anawayankha onsewo kuti: “Inetu ndikukubatizani m’madzi. Koma wina wamphamvu kuposa ine akubwera, amene ine sindili woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.+ Iyeyu adzakubatizani ndi mzimu woyera ndi moto.+ 17 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili m’manja mwake. Akufuna kuyeretseratu mbee! malo ake opunthirapo mbewu ndi kututira+ tirigu munkhokwe yake. Koma mankhusu+ adzawatentha ndi moto+ umene sungazimitsidwe.”
18 Iye anaperekanso malangizo ena ambiri ndi kupitiriza kulengeza uthenga wabwino kwa anthu. 19 Ndiyeno popeza kuti Yohane anadzudzula Herode wolamulira chigawo, pa nkhani yokhudza Herodiya, mkazi wa m’bale wake, komanso chifukwa cha zoipa zonse zimene Herode anachita,+ 20 Herode anawonjezera choipa china pa zonsezo: Anatsekera Yohane m’ndende.+
21 Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu+ nayenso anabatizidwa. Ndipo pamene anali kupemphera, kumwamba+ kunatseguka. 22 Pamenepo mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unatsika kudzamutera. Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba, akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”+
23 Pamene Yesu anayamba ntchito yake,+ anali ndi zaka pafupifupi 30.+ Anthu ankakhulupirira kuti Yesu anali
mwana wa Heli,
24 mwana wa Matati,
mwana wa Levi,
mwana wa Meliki,
mwana wa Yananai,
mwana wa Yosefe,
25 mwana wa Matatiyo,
mwana wa Amosi,
mwana wa Nahumu,
mwana wa Esili,
mwana wa Nagai,
26 mwana wa Maati,
mwana wa Matatiyo,
mwana wa Semeini,
mwana wa Yoseki,
mwana wa Yoda,
27 mwana wa Yoanani,
mwana wa Resa,
mwana wa Zerubabele,+
mwana wa Salatiyeli,+
mwana wa Neri,
28 mwana wa Meliki,
mwana wa Adi,
mwana wa Kosamu,
mwana wa Elimadama,
mwana wa Ere,
mwana wa Eliezere,
mwana wa Yorimu,
mwana wa Matati,
mwana wa Levi,
30 mwana wa Sumeoni,
mwana wa Yudasi,
mwana wa Yosefe,
mwana wa Yonamu,
mwana wa Eliyakimu,
31 mwana wa Meleya,
mwana wa Mena,
mwana wa Matata,
mwana wa Natani,+
mwana wa Davide,+
mwana wa Obedi,+
mwana wa Boazi,+
mwana wa Salimoni,+
mwana wa Naasoni,+
mwana wa Arini,+
mwana wa Hezironi,+
mwana wa Perezi,+
mwana wa Yuda,+
mwana wa Isaki,+
mwana wa Abulahamu,+
mwana wa Tera,+
mwana wa Nahori,+
mwana wa Reu,+
mwana wa Pelegi,+
mwana wa Ebere,+
mwana wa Shela,+
36 mwana wa Kainani,
mwana wa Aripakisadi,+
mwana wa Semu,+
mwana wa Nowa,+
mwana wa Lameki,+
mwana wa Inoki,+
mwana wa Yaredi,+
mwana wa Mahalaliyeli,+
mwana wa Kainani,+
mwana wa Seti,+
mwana wa Adamu,+
mwana wa Mulungu.
4 Tsopano Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndipo mzimuwo unamutenga ndi kumuyendetsa uku ndi uku m’chipululu+ 2 kwa masiku 40,+ kumene anali kuyesedwa+ ndi Mdyerekezi. Komanso m’masiku amenewo sanali kudya chilichonse, choncho masikuwo atatha, anamva njala. 3 Mdyerekezi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.” 4 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.’”+
5 Choncho anakwera naye pamwamba ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kochepa. 6 Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro+ pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.+ 7 Chotero ngati inuyo mungandiweramireko+ kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.” 8 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako+ ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+
9 Kenako anamutengera ku Yerusalemu, ndipo anamukweza pamwamba pa khoma+ la mpanda wa kachisi n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi kuchokera pano.+ 10 Pajatu Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu, kuti akutetezeni.’+ 11 Choncho, ‘Adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala uliwonse.’”+ 12 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Pajatu Malemba amati, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’”+ 13 Choncho Mdyerekeziyo atamaliza mayesero onsewo, anamusiya kufikira nthawi ina yabwino.+
14 Tsopano Yesu anabwerera ku Galileya+ atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu. Ndipo mbiri yake yabwino inamveka ponseponse m’madera onse ozungulira.+ 15 Komanso, anayamba kuphunzitsa m’masunagoge awo, ndipo anthu onse anali kumulemekeza.+
16 Kenako anabwera ku Nazareti,+ kumene analeredwa. Malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata, analowa m’sunagoge,+ ndi kuimirira kuti awerenge Malemba. 17 Pamenepo anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya. Iye anafunyulula mpukutuwo ndi kupeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18 “Mzimu wa Yehova+ uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu,+ 19 ndi kudzalalikira chaka chovomerezeka kwa Yehova.”+ 20 Atatero anapinda mpukutuwo, n’kuubwezera kwa wotumikira mmenemo ndi kukhala pansi. Maso onse m’sunagogemo anali pa iye kumuyang’anitsitsa. 21 Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”+
22 Pamenepo onse anayamba kumutamanda ndi kudabwa ndi mawu ogwira mtima+ otuluka pakamwa pake, mwakuti anali kunena kuti: “Kodi iyeyu si mwana wa Yosefe?”+ 23 Zitatero iye anawauza kuti: “Mosakayikira mawu akuti, ‘Wochiritsa+ iwe, dzichiritse wekha,’ mudzawagwiritsa ntchito pa ine. Mudzanena kuti: ‘Tinamva kuti unachita zinthu zambiri ku Kaperenao.+ Zinthu zimenezo+ uzichitenso kwanu kuno.’”+ 24 Iye ananenanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneri amene amalandiridwa kwawo. 25 Mwachitsanzo, ndikukuuzani ndithu kuti, Munali akazi ambiri amasiye mu Isiraeli m’masiku a Eliya, pamene kumwamba kunatsekedwa zaka zitatu ndi miyezi 6, mwakuti m’dziko lonse munagwa njala yaikulu.+ 26 Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akazi amenewo. M’malomwake anatumizidwa kwa mkazi wamasiye ku Zarefati+ m’dziko la Sidoni. 27 Ndiponso, munali akhate ambiri mu Isiraeli m’nthawi ya mneneri Elisa. Komabe palibe aliyense wa iwo amene anayeretsedwa, koma Namani, mwamuna wa ku Siriya.”+ 28 Tsopano onse amene anali kumvetsera mawu amenewa m’sunagogemo anakwiya kwambiri.+ 29 Iwo ananyamuka ndipo mwamsangamsanga anamutulutsira kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phiri limene anamangapo mzinda wawo, kuti akam’ponye kuphedi.+ 30 Koma iye anangodutsa pakati pawo n’kumapita.+
31 Choncho anapita ku Kaperenao,+ mzinda wa ku Galileya. Ndipo anali kuwaphunzitsa pa sabata. 32 Kumeneko anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa anali kulankhula ndi mphamvu za ulamuliro.+ 33 Tsopano m’sunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu,+ chiwanda chonyansa, ndipo anafuula ndi mawu amphamvu kuti: 34 “Tili nanu chiyani,+ Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani+ bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu.”+ 35 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye.” Choncho chiwandacho chinagwetsa munthuyo pansi pakati pawo, kenako chinatuluka mwa iye osamuvulaza.+ 36 Ataona zimenezi, onse anadabwa kwambiri, ndipo anayamba kukambirana kuti: “Kulankhula kumeneku ndi kwa mtundu wanji anthuni? Taonani! Akutha kudzudzula mizimu yonyansa mwa ulamuliro ndi mphamvu, ndipo mizimuyo ikutulukadi.”+ 37 Choncho mbiri yake inapitiriza kufalikira ponseponse m’midzi yonse yozungulira.+
38 Atatuluka m’sunagogemo, anakalowa m’nyumba ya Simoni. Kumeneko apongozi aakazi a Simoni anali kudwala malungo* aakulu, choncho anam’pempha kuti apite kumeneko chifukwa cha mayiwo.+ 39 Chotero anaima pamene mayiwo anagona ndi kuwachiritsa,+ ndipo malungowo anatheratu. Nthawi yomweyo mayiwo anadzuka n’kuyamba kuwatumikira.+
40 Koma pamene dzuwa linali kulowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa mwa kuika manja ake pa aliyense.+ 41 Ziwanda nazonso zinatuluka mwa anthu ambiri.+ Zinali kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana+ wa Mulungu.” Koma iye anali kudzudzula ziwandazo, ndipo sanali kuzilola kuti zilankhule,+ chifukwa zinali kudziwa kuti iye+ ndi Khristu.+
42 Kutacha, anatuluka ndi kupita kumalo kopanda anthu.+ Koma khamu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anayesa kumuletsa kuti asawasiye. 43 Koma iye anawauza kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.”+ 44 Choncho anapita n’kumalalikira m’masunagoge a mu Yudeya.+
5 Nthawi inayake khamu la anthu linali kumvetsera pamene Yesu anali kuphunzitsa mawu a Mulungu m’mphepete mwa nyanja ya Genesarete.*+ Kenako anthuwo anayamba kumupanikiza. 2 Pamenepo iye anaona ngalawa ziwiri atazikocheza m’mphepete mwa nyanjayo, koma asodzi anali atatsikamo ndipo anali kutsuka maukonde awo.+ 3 Choncho iye analowa m’ngalawa imodzi, imene inali ya Simoni, ndipo anamupempha kuti aisunthire m’madzi pang’ono. Kenako anakhala pansi, ndipo ali m’ngalawamo+ anayamba kuphunzitsa khamu la anthulo. 4 Atamaliza kulankhula, anauza Simoni kuti: “Palasira kwakuya, ndipo muponye maukonde+ anu kuti muphe nsomba.” 5 Koma poyankha Simoni anati: “Mlangizi, ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kalikonse.+ Koma popeza mwanena ndinu, ndiponya maukondewa.” 6 Atachita zimenezo, anakola nsomba zochuluka kwambiri. Ndipo maukonde awo anayamba kung’ambika. 7 Choncho anakodola anzawo amene anali m’ngalawa ina kuti adzawathandize.+ Iwo anabweradi, ndipo nsombazo zinadzaza ngalawa zonse ziwiri, moti ngalawazo zinayamba kumira. 8 Ataona zimenezi, Simoni Petulo+ anagwada ndi kuweramira pamawondo a Yesu n’kumuuza kuti: “Ambuye, chokani pali ine pano, chifukwa ndine munthu wochimwa.”+ 9 Simoni anadabwa kwambiri ndi nsomba zimene anaphazo, chimodzimodzi ena onse amene anali naye limodzi. 10 Komanso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo,+ amene anali kugwirizana ndi Simoni anadabwa kwambiri. Koma Yesu anauza Simoni kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”+ 11 Choncho ngalawazo anafika nazo kumtunda, ndipo iwo anasiya chilichonse ndi kumutsatira.+
12 Nthawi inanso pamene anali mumzinda wina, anakumana ndi munthu wakhate thupi lonse. Pamene anaona Yesu, munthuyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kum’pempha, kuti: “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 13 Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+ 14 Kenako analamula munthuyo kuti asauze aliyense.+ Ndiyeno anamuuza kuti: “Koma upite ukadzionetse kwa wansembe,+ ndipo ukapereke nsembe+ ya kuyeretsedwa kwako, monga mmene Mose analamulira, kuti ikhale umboni kwa iwo.”+ 15 Koma mbiri yake inali kufalikira kwambiri, ndipo makamu a anthu anali kusonkhana pamodzi kudzamumvetsera ndi kudzachiritsidwa matenda awo.+ 16 Koma iye anakhalabe kwayekha m’chipululu ndi kupitiriza kupemphera.+
17 Tsiku lina iye anali kuphunzitsa, ndipo Afarisi ndi aphunzitsi a chilamulo ochokera m’midzi yonse ya Galileya, ku Yudeya ndi ku Yerusalemu anakhala pansi pamalo omwewo. Ndipo mphamvu ya Yehova inali pa iye kuti athe kuchiritsa.+ 18 Kenako panafika anthu atanyamula munthu wakufa ziwalo pakabedi. Iwo anali kufunafuna njira yoti amulowetsere ndi kumuika pafupi ndi Yesu.+ 19 Koma atalephera kudutsa naye chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, anakwera padenga.* Ndipo kudzera pabowo limene anatsegula padengapo, anamutsitsa limodzi ndi kabediko n’kumufikitsa pakati pa anthu amene anali pamaso pa Yesu.+ 20 Ataona chikhulupiriro chawo, anati: “Bwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+ 21 Pamenepo alembi ndi Afarisi anayamba kudzifunsa, kuti: “Ndani ameneyu kuti azinyoza Mulungu chonchi?+ Winanso ndani amene angakhululukire machimo? Si Mulungu yekha kodi?”+ 22 Koma Yesu, pozindikira zimene anali kuganiza anawayankha kuti: “Kodi mukuganiza chiyani m’mitima mwanu?+ 23 Chapafupi n’chiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka uyende’?+ 24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo . . .” anauza munthu wakufa ziwalo uja kuti: “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga kabedi kakoka uzipita kwanu.”+ 25 Nthawi yomweyo anaimirira onse akuona, ndipo ananyamula chogonera chake chija n’kupita kwawo, akutamanda Mulungu.+ 26 Pamenepo anthu onsewo anadabwa kwambiri,+ ndipo anayamba kutamanda Mulungu, mwakuti anagwidwa ndi mantha. Iwo anali kunena kuti: “Taona zodabwitsa lero!”+
27 Zimenezi zitachitika iye anachokako. Kenako anaona wokhometsa msonkho wotchedwa Levi atakhala pansi mu ofesi yokhomera msonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ 28 Pamenepo Leviyo anasiya chilichonse,+ ndipo ananyamuka n’kumutsatira. 29 Tsopano Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Kumeneko kunali khamu lalikulu la okhometsa msonkho ndi ena ambiri, ndipo anali kudyera limodzi.+ 30 Afarisi ndi alembi awo ataona izi, anayamba kung’ung’udza ndi kufunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?”+ 31 Poyankha, Yesu anawauza kuti: “Anthu athanzi safuna dokotala,+ koma odwala ndi amene amamufuna.+ 32 Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.”+
33 Iwo anamuuza kuti: “Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri ndi kupemphera mopembedzera. Ophunzira a Afarisi amachitanso chimodzimodzi, koma anuwa amangodya ndi kumwa.”+ 34 Yesu anawayankha kuti: “Inu simungauze anzake a mkwati kuti asale kudya pamene mkwatiyo ali nawo limodzi, mungatero ngati?+ 35 Koma masiku adzafika pamene mkwati+ adzachotsedwa pakati pawo.+ Pamenepo iwo adzasala kudya masiku amenewo.”+
36 Komanso, anawapatsa fanizo kuti: “Palibe amene amadula chigamba pamalaya akunja atsopano n’kuchisokerera pamalaya akunja akale. Munthu akachita zimenezo, chigamba chatsopanocho chimachoka pansalu yakaleyo. Ndiponso chigamba cha nsalu yatsopanocho sichiyenerana ndi malaya akalewo.+ 37 Komanso, palibe amene amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Munthu akachita zimenezo, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba achikopawo.+ Vinyoyo amatayika ndipo matumba achikopawo amawonongeka.+ 38 Koma vinyo watsopano ayenera kuikidwa m’matumba achikopa atsopano. 39 Munthu akamwa vinyo wakale safunanso watsopano, chifukwa amanena kuti, ‘Wakaleyu+ ali bwino kwambiri.’”
6 Tsiku lina pa sabata, Yesu anali kudutsa m’munda wa tirigu, ndipo ophunzira ake anali kubudula+ ngala za tirigu. Anali kuzifikisa m’manja mwawo n’kumadya.+ 2 Afarisi ena ataona zimenezi anati: “N’chifukwa chiyani mukuchita zosemphana ndi malamulo+ pa sabata?”+ 3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide+ anachita pamene iye ndi amuna amene anali naye anamva njala?+ 4 Kodi simunawerenge kuti analowa m’nyumba ya Mulungu ndi kutenga mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu+ n’kudya, ndipo ina anapatsa amuna amene anali naye limodzi? Malamulo salola aliyense kudya mkate umenewu koma ansembe okha.”+ 5 Kenako anapitiriza kuwauza kuti: “Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa sabata.”+
6 Tsiku linanso la sabata,+ iye analowa m’sunagoge n’kuyamba kuphunzitsa. Mmenemo munali munthu amene dzanja lake lamanja linali lopuwala.+ 7 Alembi ndi Afarisi anali kumuyang’anitsitsa+ tsopano, kuti aone ngati angachiritse munthu pa sabata. Iwo anali n’cholinga chakuti am’peze chifukwa.+ 8 Koma iye anadziwa zimene iwo anali kuganiza.+ Choncho anauza munthu wa dzanja lopuwalayo kuti: “Nyamuka, uimirire pakatipa.” Munthuyo ananyamuka n’kuima chilili.+ 9 Pamenepo Yesu anawafunsa kuti: “Ndikufunseni anthu inu, Kodi malamulo amalola kuchita chiti pa sabata? Chabwino kapena choipa?+ Kupulumutsa moyo kapena kuuwononga?”+ 10 Atamwaza maso uku ndi uku kuwayang’ana onsewo, anauza munthu uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” Munthuyo anachitadi zimenezo, ndipo dzanja lakelo linakhalanso labwinobwino.+ 11 Koma iwo anapenga ndi mkwiyo ndipo anayamba kukambirana zoti amuchite Yesu.+
12 M’masiku amenewa, Yesu anapita kuphiri kukapemphera,+ ndipo anachezera kupemphera kwa Mulungu usiku wonse.+ 13 Kutacha, anaitana ophunzira ake ndi kusankha 12 pakati pawo. Amenewa anawatcha “atumwi.”+ 14 Iye anasankha Simoni, amenenso anam’patsa dzina lakuti Petulo,+ ndi m’bale wake Andireya. Anasankhanso Yakobo ndi Yohane,+ Filipo+ ndi Batolomeyo, 15 Mateyu ndi Tomasi,+ Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa “wachangu.”+ 16 Komanso anasankha Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anam’pereka.+
17 Kenako anatsika nawo ndi kuima pamalo am’munsi, athyathyathya. Pamenepo panali khamu lalikulu la ophunzira ake. Panalinso chikhamu cha anthu+ ochokera ku Yudeya konse ndi ku Yerusalemu konse, komanso kumadera am’mphepete mwa nyanja a ku Turo ndi ku Sidoni. Onsewo anabwera kudzamumvetsera ndi kudzachiritsidwa matenda awo.+ 18 Ngakhalenso amene anali kusautsidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa. 19 Onse m’khamulo anali kuyesetsa kuti amukhudze,+ chifukwa mphamvu+ zinali kutuluka mwa iye ndi kuchiritsa onsewo.
20 Pamenepo anakweza maso ake ndi kuyang’ana ophunzira ake, ndipo anawauza kuti:+
“Odala ndinu osaukanu,+ chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.
21 “Inu amene mukumva njala+ tsopano ndinu odala, chifukwa mudzakhuta.+
“Inu amene mukulira tsopano ndinu odala, chifukwa mudzaseka.+
22 “Ndinu odala anthu akamadana nanu,+ kukusalani, kukunyozani ndi kukana+ dzina lanu n’kumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu. 23 Kondwerani pa tsiku limenelo ndi kudumphadumpha, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti zomwezo ndi zimenenso makolo awo akale anachitira aneneri.+
24 “Koma tsoka inu anthu achuma,+ chifukwa mwalandiriratu zonse zokusangalatsani.+
25 “Tsoka inu amene mukukhuta tsopano, chifukwa mudzamva njala.+
“Tsoka inu amene mukuseka tsopano, chifukwa mudzamva chisoni ndi kulira.+
26 “Muli ndi tsoka, anthu onse akamanena zabwino za inu, pakuti zoterezi n’zimene makolo awo akale anachitira aneneri onyenga.+
27 “Koma inu amene mukumvetseranu ine ndikukuuzani kuti, Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kuchita zabwino+ kwa amene akudana nanu. 28 Pitirizani kudalitsa okutembererani ndi kupempherera amene akukunyozani.+ 29 Amene wakumenya patsaya ili,+ um’patsenso linalo. Amene wakulanda+ malaya ako akunja, usamuletse kutenga malaya ako amkati. 30 Aliyense amene wakupempha kanthu mupatse,+ ndipo amene wakulanda zinthu usamuumirize kuti abweze.
31 “Komanso, zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.+
32 “Kodi mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, mudzapeza phindu lotani? Pakuti ngakhale ochimwa amakonda amene amawakonda.+ 33 Ngati mumachita zabwino kwa okhawo amene amakuchitirani zabwino, mudzapindulanji kwenikweni? Pakuti ngakhale ochimwa amachita zomwezo.+ 34 Komanso, ngati mumakongoza popanda chiwongoladzanja+ kwa okhawo amene mukuyembekezera kuti adzabweza ngongoleyo, mudzapindulanji? Ochimwanso amakongoza ochimwa anzawo popanda chiwongoladzanja, kuti adzawabwezere zomwezo.+ 35 Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu. Pitirizani kuchita zabwino, ndi kukongoza+ popanda chiwongoladzanja, osayembekezera kulandira kalikonse. Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wam’mwambamwamba,+ chifukwa iye ndi wachifundo+ kwa osayamika ndi kwa oipa. 36 Pitirizani kukhala achifundo, potengera Atate wanu amenenso ali wachifundo.+
37 “Komanso, lekani kuweruza ena, mukatero inunso simudzaweruzidwa.+ Lekani kutsutsa ena, ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitirizani kukhululukira anthu machimo awo ndipo machimo anunso adzakhululukidwa.+ 38 Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.+ Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”+
39 Kenako anawauzanso fanizo lakuti: “Wakhungu sangatsogolere wakhungu mnzake, angatero ngati? Ngati atatero onse awiri angagwere m’dzenje, si choncho kodi?+ 40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake.+ 41 Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako, koma osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli m’diso lako?+ 42 Ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘M’bale, taima ndikuchotse kachitsotso kamene kali m’diso lakoka,’ koma iwe osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli m’diso lako?+ Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo,+ ndipo ukatero udzatha kuona bwinobwino mmene ungachotsere kachitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako.+
43 “Kulibe mtengo wabwino umene ungabale chipatso chowola. Ndipo palibe mtengo wowola umene ungabale chipatso chabwino.+ 44 Pakuti mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake.+ Mwachitsanzo, anthu sathyola nkhuyu mumtengo waminga, kapena kudula mphesa m’chitsamba chaminga.+ 45 Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino+ cha mtima wake. Koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma chake choipa, pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+
46 “Nanga n’chifukwa chiyani mumandiitana kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osachita zimene ndimanena?+ 47 Aliyense wobwera kwa ine kudzamva mawu anga, ndi kuwachita, ndikuuzani amene amafanana naye:+ 48 Iyeyo ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama kwambiri ndi kuyala maziko pathanthwe. Ndipo pamene mtsinje unasefukira,+ madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza, chifukwa anaimanga bwino.+ 49 Koma amene akumva ndi kusachita,+ ali ngati munthu womanga nyumba yopanda maziko padothi. Apanso mtsinje unasefukira n’kuwomba nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo inagwa, mwakuti kugwa+ kwa nyumba imeneyo kunali kwamkokomo.”+
7 Yesu atamaliza mawu ake onse amene anthu anali kumvetsera, analowa mumzinda wa Kaperenao.+ 2 Kumeneko kapolo wa kapitawo wina wa asilikali, amene kapitawoyo anali kum’konda kwambiri, anali kudwala ndipo anali pafupi kumwalira.+ 3 Kapitawoyo atamva za Yesu, anatumiza akulu a Ayuda kwa iye kukam’pempha kuti abwere kudzapulumutsa kapolo wakeyo. 4 Choncho anthuwo atafika kwa Yesu anayamba kum’chonderera ndi mtima wonse, kuti: “N’ngoyeneradi kuti mum’thandize, 5 chifukwa amakonda anthu amtundu wathu+ ndipo anatimangira sunagoge.” 6 Choncho Yesu ananyamuka nawo limodzi. Koma atatsala pang’ono kufika kunyumbako, anakumana ndi mabwenzi a kapitawo wa asilikali uja, amene anawatuma kuti adzamuuze kuti: “Mbuyanga, musavutike, pakuti ine sindili woyenera kuti inu mulowe m’nyumba mwanga.+ 7 N’chifukwa chake inenso sindinabwere kwa inu, poona kuti ndine wosayenera kutero. Koma mungonena mawu okha ndipo mtumiki wanga achira. 8 Pakuti inenso ndili ndi akuluakulu ondiyang’anira, komanso ndili ndi asilikali amene ali pansi panga. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’ amapita, wina ndikamuuza kuti ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.”+ 9 Yesu atamva zimenezi anadabwa ndi munthu ameneyu. Kenako anacheukira khamu la anthu omutsatira aja n’kunena kuti: “Kunena zoona, ngakhale mu Isiraeli sindinapezemo chikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.”+ 10 Koma amene anatumidwa aja atabwerera kunyumba, anapeza kapolo uja ali bwinobwino.+
11 Patangopita kanthawi pang’ono, ananyamuka kupita kumzinda wotchedwa Naini. Ophunzira ake ndi khamu lalikulu la anthu anayenda naye limodzi. 12 Atayandikira pachipata cha mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula maliro.+ Womwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo+ kwa mayi ake. Komanso mayi akewo anali mkazi wamasiye. Khamu lalikulu ndithu la anthu ochokera mumzindawo linali limodzi ndi mayiwo. 13 Pamene Ambuye anaona mayiwo, anawamvera chifundo,+ ndipo anawauza kuti: “Tontholani mayi.”+ 14 Atatero anayandikira ndi kugwira chithathacho. Pamenepo onyamulawo anangoima chilili, ndipo iye anati: “Mnyamata iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!”+ 15 Pamenepo wakufayo anadzuka ndi kukhala tsonga, ndipo anayamba kulankhula. Kenako anam’pereka kwa mayi ake.+ 16 Zitatero anthu onse anagwidwa ndi mantha,+ moti anayamba kutamanda Mulungu, kuti: “Mneneri wamkulu+ waonekera pakati pathu.” Analinso kunena kuti, “Mulungu wacheukira anthu ake.”+ 17 Nkhani imeneyi yonena za Yesu inafala ponseponse mu Yudeya monse ndi m’madera onse ozungulira.
18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza zonsezi.+ 19 Choncho Yohane anaitanitsa ophunzira ake awiri ndi kuwatuma kwa Ambuye kukafunsa kuti: “Kodi Mesiya* amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?”+ 20 Atafika kwa iye amunawo anati: “Yohane M’batizi watituma kudzakufunsani kuti: ‘Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?’” 21 Mu ola limenelo iye anachiritsa nthenda zambiri+ ndi anthu ambiri odwala mwakayakaya ndi kutulutsa mizimu yoipa. Ndipo anachiritsa akhungu ochuluka moti anayamba kuona. 22 Choncho poyankha anauza amuna awiri aja kuti: “Pitani+ mukamuuze Yohane zimene mwaona ndi kumva: Akhungu+ akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa, ogontha akumva, akufa akuukitsidwa ndipo aumphawi akumva+ uthenga wabwino.+ 23 Wodala ndi amene sanapunthwe chifukwa cha ine.”+
24 Amithenga a Yohane aja atachoka, iye anayamba kuuza khamu la anthulo za Yohane kuti: “Kodi munapita m’chipululu kukaona chiyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+ 25 Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena?+ Iyayi, pajatu ovala zovala zapamwamba ndiponso amoyo wamwanaalirenji amakhala m’nyumba zachifumu.+ 26 Nangano munapita kukaona chiyani makamaka? Mneneri kapena?+ Inde, ndikukuuzani, woposadi mneneri.+ 27 Malemba amanena za iyeyu kuti, ‘Taona! Inetu ndikutumiza mthenga wanga choyamba,+ amene adzakukonzera njira.’+ 28 Ndithudi ndikukuuzani, Mwa onse obadwa mwa akazi, palibe wamkulu+ woposa Yohane. Koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu wa Mulungu ndiye wamkulu kuposa iyeyu.”+ 29 (Pamenepo anthu onse ndi okhometsa msonkho omwe atamva zimenezi, analengeza kuti Mulungu ndi wolungama,+ popeza iwo anali atabatizidwa ndi ubatizo wa Yohane.+ 30 Koma Afarisi ndi anthu odziwa Chilamulo ananyalanyaza malangizo+ amene Mulungu anawapatsa. Choncho Yohane sanawabatize.)
31 “Kodi anthu a m’badwo uwu ndiwayerekeze ndi ndani, ndipo akufanana ndi ndani?+ 32 Iwo ali ngati ana aang’ono amene akhala pansi mumsika n’kumafuulirana kuti, ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunalire.’+ 33 Mofanana ndi zimenezi, Yohane M’batizi anabwera ndipo sadya chakudya kapena kumwa vinyo, koma inu mumanena kuti, ‘Ali ndi chiwanda.’+ 34 Kunabwera Mwana wa munthu ndipo iye akudya ndi kumwa, koma inu mumati, ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa!’+ 35 Mulimonsemo, nzeru+ imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.”+
36 Tsopano Mfarisi wina anaumiriza Yesu kuti akadye naye. Choncho anapita kunyumba+ ya Mfarisiyo ndipo anamupatsa chakudya. 37 Koma mayi wina amene anali wodziwika mumzindawo kuti ndi wochimwa, anamva kuti Yesu akudya chakudya m’nyumba ya Mfarisi. Choncho anapita komweko ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala,+ muli mafuta onunkhira. 38 Atafika anagwada kumapazi kwake ndi kuyamba kulira, mwakuti anayamba kunyowetsa mapazi ake ndi misozi, kwinaku akupukuta mapaziwo ndi tsitsi la m’mutu mwake. Komanso anapsompsona mapazi akewo mwachikondi ndi kuwapaka mafuta onunkhirawo. 39 Mfarisi amene anamuitana uja ataona izi, mumtima mwake anati: “Munthu uyu akanakhala mneneri,+ akanadziwa kuti mkazi amene akumugwirayu ndi ndani, ndiponso kuti ndi wotani. Akanadziwa kuti ndi wochimwa.”+ 40 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Simoni, ndikufuna ndikuuze kanthu kena.” Iye anati: “Ndiuzeni Mphunzitsi!”
41 “Amuna awiri anatenga ngongole kwa munthu wina wokongoza ndalama. Mmodzi anatenga ngongole ya madinari 500,+ koma winayo anatenga ngongole ya madinari 50. 42 Atasowa chopereka kuti abweze ngongolezo, mwiniwake uja anakhululukira+ onsewo ndi mtima wonse. Kodi ndani mwa awiriwo amene angam’konde kwambiri?” 43 Poyankha Simoni anati: “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira zochulukayo.” Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola.” 44 Atatero anacheukira mayi uja ndi kuuza Simoni kuti: “Ukumuona kodi mayi uyu? Ngakhale kuti ndalowa m’nyumba yako, sunandipatse madzi+ otsukira mapazi anga. Koma mayi uyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuipukuta ndi tsitsi lake. 45 Iwe sunandipsompsone,+ koma chilowereni muno, mayiyu sanaleke kupsompsona mapazi anga mwachikondi. 46 Iwe sunathire mafuta m’mutu mwanga,+ koma mayiyu wapaka mapazi anga mafuta onunkhira. 47 Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuza kuti, machimo ake akhululukidwa,+ ngakhale kuti ndi ochuluka. N’chifukwa chake akusonyeza chikondi chochuluka. Koma amene wakhululukidwa machimo ochepa amasonyezanso chikondi chochepa.” 48 Kenako anauza mayiyo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.”+ 49 Pamenepo onse amene anakhala naye patebulopo anayamba kudzifunsa mumtima mwawo kuti: “Kodi munthu ameneyu n’ngotani wokhozanso ngakhale kukhululukira machimo?”+ 50 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa.+ Pita mu mtendere.”+
8 Mosakhalitsa, Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira+ ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi. 2 Analinso ndi amayi+ ena amene anawatulutsa mizimu yoipa ndi kuwachiritsa matenda awo. Ena mwa iwo anali Mariya wotchedwanso Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7.+ 3 Jowana+ mkazi wa Kuza kapitawo wa Herode, Suzana ndi amayi ena ambiri, amene anali kutumikira Yesu ndi atumwiwo pogwiritsa ntchito chuma chawo.
4 Ndiyeno khamu lalikulu la anthu litasonkhana, limodzi ndi ena amene anali kumulondola kuchokera m’mizinda yosiyanasiyana, Yesu anawafotokozera fanizo kuti:+ 5 “Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu zake. Pamene anali kufesa, zina zinagwera m’mbali mwa msewu ndipo zinapondedwapondedwa, kenako zinadyedwa ndi mbalame zam’mlengalenga.+ 6 Zina zinagwera pathanthwe. Koma zitamera, zinauma chifukwa panalibe chinyontho.+ 7 Zinanso zinagwera paminga. Mingazo zinali kukulira limodzi ndi mbewuzo ndipo zinalepheretsa mbewuzo kukula.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino, ndipo zitakula, zinabala zipatso kuwirikiza maulendo 100.”+ Atanena zimenezi, analankhula mokweza mawu kuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+
9 Koma ophunzira ake anayamba kumufunsa tanthauzo la fanizo limeneli.+ 10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira zinsinsi zopatulika za ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawo, zonse ndi mafanizo okhaokha.+ Izi zili choncho kuti kuona aziona ndithu, koma kukhale kopanda phindu, kumvanso azimva ndithu, koma asazindikire tanthauzo lake.+ 11 Koma fanizoli+ tanthauzo lake ndi ili: Mbewuzo ndi mawu a Mulungu.+ 12 Zogwera m’mbali mwa msewuzo ndi anthu amene amamva mawuwo.+ Kenako Mdyerekezi+ amabwera ndi kudzachotsa mawuwo m’mitima yawo kuti asakhulupirire ndi kupulumuka.+ 13 Zogwera pathanthwe ndi anthu amene amati akangomva mawuwo, amawalandira ndi chimwemwe, koma oterewa alibe mizu. Amakhulupirira kwa kanthawi, koma nthawi yoyesedwa ikafika amagwa.+ 14 Zimene zinagwera paminga, ndi anthu amene amva mawu a Mulungu. Koma chifukwa chotengeka ndi nkhawa, chuma ndi zosangalatsa za moyo uno,+ amalephera kukula bwino, ndipo zipatso zawo sizikhwima.+ 15 Komano zogwera panthaka yabwino, ndi anthu amene pambuyo pomva mawuwo ndi mtima woona+ komanso wabwino, amawagwiritsitsa ndi kubereka zipatso mwa kupirira.+
16 “Palibe amene amati akayatsa nyale, amaivundikira ndi chiwiya kapena kuiika pansi pa bedi. Koma amaiika pachoikapo nyale kuti amene akulowa aone kuwala.+ 17 Chilichonse chobisidwa+ chidzaonekera poyera. Ndipo zinthu zonse zosungidwa mwachinsinsi kwambiri zidzadziwika ndi kuululika.+ 18 Choncho muzimvetsera mwatcheru kwambiri. Pakuti amene ali nazo, adzapatsidwa zochuluka,+ koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene akuganizira kuti ali nazo.”+
19 Tsopano mayi ake ndi abale ake+ anabwera kumeneko, koma chifukwa cha khamu la anthu, analephera kufika kumene iyeyo anali.+ 20 Koma ena anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu aima panjapo akufuna kuonana nanu.”+ 21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndi awa amene amamvetsera mawu a Mulungu ndi kuwachita.”+
22 Tsiku lina m’masiku amenewo Yesu ndi ophunzira ake anakwera ngalawa, ndipo anawauza kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Pamenepo iwo anayamba kupalasa.+ 23 Koma ulendowo uli mkati Yesu anagona tulo. Kenako panyanjapo panayamba kuwomba mphepo yamkuntho, ndipo madzi anayamba kudzaza m’ngalawamo moti akanatha kumira.+ 24 Kenako anapita kwa iye kukam’dzutsa. Iwo anati: “Mlangizi, Mlangizi, tikufa!”+ Chotero iye anadzuka ndi kudzudzula+ mphepo ndi mafunde amphamvuwo, mwakuti zinaleka, ndipo panachita bata. 25 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo anagwidwa ndi mantha ndipo anathedwa nzeru, mwakuti anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani kwenikweni, wochita kulamula mphepo ndi madzi ndipo n’kumumvera?”+
26 Ndiyeno anakocheza m’dera la Agerasa, tsidya linalo, moyang’anana ndi Galileya.+ 27 Koma atangotsika n’kufika kumtunda, anakumana ndi munthu wina waziwanda wochokera mumzindawo. Kwa nthawi yaitali ndithu, munthuyo anali kungokhala osavala, komanso sanali kukhala kunyumba, koma kumanda.+ 28 Ataona Yesu anafuula kwambiri ndi kudzigwetsa pansi pamaso pake. Kenako anafuula ndi mawu amphamvu kuti: “Kodi ndili nanu chiyani,+ Yesu, Mwana wa Mulungu Wam’mwambamwamba? Chonde, chonde, musandizunze.”+ 29 (Pakuti iye anali kuuza mzimu wonyansawo kuti utuluke mwa munthuyo. Mzimu umenewu unamugwira mwamphamvu+ kwa nthawi yaitali ndithu. Mobwerezabwereza anali kumumanga ndi maunyolo komanso matangadza n’kumamuyang’anira. Koma chifukwa cha mphamvu ya chiwandacho, anali kudula maunyolowo ndi kuthawira kumalo opanda anthu.) 30 Yesu anamufunsa kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti: “Khamu,” chifukwa mwa iye munalowa ziwanda zambiri.+ 31 Ziwandazo zinali kumuchonderera+ kuti asazilamule kuti zipite kuphompho.+ 32 Tsopano gulu lalikulu ndithu la nkhumba+ linali kudya paphiri kumeneko. Chotero ziwandazo zinamuchonderera kuti azilole kukalowa munkhumbazo.+ Ndipo iye anazilola. 33 Choncho ziwandazo zinatuluka mwa munthuyo ndi kukalowa munkhumbazo. Pamenepo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi ndi kulumphira m’nyanja ndipo zinamira.+ 34 Koma oyang’anira ziwetozo ataona zimene zinachitikazo, anathawa ndi kukanena zimenezi mumzinda ndi m’midzi.+
35 Zitatero anthu anabwera kudzaona zomwe zachitikazo. Atafika kwa Yesu anapeza munthu amene anam’tulutsa ziwanda uja atakhala pansi pafupi ndi Yesu. Anamupeza atavala bwino komanso maganizo ake ali bwinobwino, ndipo iwo anachita mantha.+ 36 Amene anaona zochitikazo anawafotokozera mmene munthu wogwidwa ziwandayo anam’chiritsira.+ 37 Choncho khamu lonse lochokera m’midzi yapafupi ya Agerasa linam’pempha kuti achoke kwawoko, chifukwa linagwidwa ndi mantha aakulu.+ Pamenepo iye anakwera ngalawa kuti azipita. 38 Ndiyeno munthu amene anam’tulutsa ziwanda uja anapempha kuti aziyenda naye. Koma Yesu anauza munthuyo kuti apite kwawo. Iye anati:+ 39 “Pita kunyumba, ndipo ukafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.”+ Munthu uja anapitadi, ndipo anali kufalitsa mumzinda wonsewo zimene Yesu anam’chitira.+
40 Yesu atabwerera ku Galileya, khamu la anthu linamulandira ndi manja awiri, chifukwa onse anali kumuyembekeza.+ 41 Kenako panafika munthu wina dzina lake Yairo. Iyeyu anali mtsogoleri wa sunagoge. Ndiyeno anadzigwetsa pamapazi a Yesu ndi kum’chonderera kuti akalowe m’nyumba yake.+ 42 Yairo anachita zimenezi chifukwa mwana wake wamkazi wazaka pafupifupi 12, mwana yekhayo amene anali naye, anali pafupi kumwalira.+
Pamene anali kupita anthu ambiri anakhamukira komweko.+ 43 Ndiyeno panali mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi+ kwa zaka 12, ndipo palibe aliyense amene anatha kum’chiritsa.+ 44 Mayiyu anamudzera kumbuyo Yesu n’kugwira ulusi wopota wa m’mphepete+ mwa malaya ake akunja.+ Nthawi yomweyo anasiya kutaya magazi.+ 45 Pamenepo Yesu anati: “Ndani wandigwira?”+ Onse atakana, Petulo anati: “Mlangizi, anthu onsewa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.”+ 46 Koma Yesu anati: “Wina wandigwira, chifukwa ndamva kuti mphamvu+ yatuluka mwa ine.”+ 47 Mayiyo ataona kuti zimene wachitazo zadziwika anapita kwa Yesu akunjenjemera, ndipo anagwada ndi kuulula pamaso pa anthu onse chimene chinam’chititsa kuti amugwire, komanso mmene wachirira nthawi yomweyo.+ 48 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.+ Pita mu mtendere.”+
49 Ali mkati molankhula, panafika nthumwi ya mtsogoleri wa sunagoge uja, ndipo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira. Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.”+ 50 Yesu atamva zimenezi, anamuyankha kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi,+ ndipo mwana wako apulumuka.” 51 Atafika kunyumbako sanalole kuti aliyense alowe naye kupatulapo Petulo, Yohane ndi Yakobo, komanso bambo ndi mayi a mtsikanayo.+ 52 Koma anthu onse anali kulira ndi kudziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni. Choncho Yesu anawauza kuti: “Tontholani,+ pakuti mwanayu sanamwalire ayi, koma akugona.”+ 53 Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kumuseka monyodola, chifukwa anali kudziwa kuti wamwalira.+ 54 Koma iye anamugwira dzanja ndi kuitana kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!”+ 55 Pamenepo mzimu wake+ unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anadzuka.+ Ndiyeno anawauza kuti am’patse chakudya mtsikanayo.+ 56 Pamenepo, makolo akewo anakondwa kwambiri, koma Yesu anawalangiza kuti asauze aliyense zimene zachitikazo.+
9 Tsopano Yesu anasonkhanitsa atumwi 12 aja ndi kuwapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse ndi kuti azitha kuchiritsa matenda.+ 2 Choncho anawatumiza kukalalikira ufumu wa Mulungu ndi kuchiritsa anthu. 3 Iye anawauza kuti: “Musanyamule kanthu pa ulendowu, musatenge ndodo, kapena thumba la chakudya, kapena mkate, kapena ndalama zasiliva, kapena kutenga malaya awiri amkati.+ 4 Koma mukafika pakhomo lililonse, khalani pamenepo kufikira nthawi yochoka kumeneko.+ 5 Kulikonse kumene anthu sakakulandirani, potuluka mumzinda+ umenewo, sansani fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni wowatsutsa.”+ 6 Pamenepo ananyamuka ndi kulowa m’deralo m’mudzi ndi mudzi. Iwo anali kulengeza uthenga wabwino ndi kuchiritsa anthu kwina kulikonse.+
7 Tsopano Herode* wolamulira chigawo anamva zonse zimene zinali kuchitika. Iye anathedwa nzeru chifukwa ena anali kunena kuti Yohane anauka kwa akufa.+ 8 Koma ena anali kunena kuti Eliya waonekera. Enanso anali kunena kuti winawake mwa aneneri akale wauka. 9 Ndiyeno Herode anati: “Yohane ndinamudula mutu.+ Nanga uyu ndaninso amene akuchita zomwe ndikumvazi?” Choncho anali kufunitsitsa kumuona.+
10 Atumwi aja atabwerako anafotokozera Yesu zimene iwo anachita.+ Atatero anawatenga ndi kupita nawo kwaokhaokha+ mumzinda wotchedwa Betsaida. 11 Koma khamu la anthu linadziwa ndi kum’tsatira. Iye anawalandirabe bwino ndi kuyamba kuwauza za ufumu wa Mulungu,+ ndipo anachiritsa amene anafunika kuchiritsidwa.+ 12 Komano nthawi inali itapita. Choncho atumwi 12 aja anafika ndi kumuuza kuti: “Auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite m’midzi ndi m’madera apafupi kuti akapeze malo ogona ndi chakudya, chifukwa kumene tili kuno n’kopanda anthu.”+ 13 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.”+ Iwo anati: “Tilibe chilichonse kuno koma mitanda ya mkate isanu ndi nsomba+ ziwiri zokha basi. Mwina tingapite kukagula chakudya chokwanira anthu onsewa.”+ 14 Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000.+ Koma Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Auzeni akhale m’magulu, muja amakhalira akamadya chakudya. Pagulu lililonse pakhale anthu pafupifupi 50.”+ 15 Iwo anachitadi zimenezo, mwakuti onsewo anawakhazika bwinobwino. 16 Kenako anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija ndipo anayang’ana kumwamba ndi kudalitsa chakudyacho. Kenako ananyemanyema mitanda ya mkate ndi nsombazo n’kupereka kwa ophunzira kuti apatse anthuwo.+ 17 Choncho onse anadya ndi kukhuta, ndipo anatolera zotsala kudzaza madengu 12.+
18 Nthawi inayake, pamene anali kupemphera payekha, ophunzira ake anafika kwa iye onse pamodzi. Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi anthuwa akumati ine ndine ndani?”+ 19 Poyankha iwo anati: “Amati ndinu Yohane M’batizi. Koma ena amati ndinu Eliya. Enanso amati mmodzi wa aneneri akale wauka.”+ 20 Pamenepo anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha kuti:+ “Ndinu Khristu+ wa Mulungu.” 21 Ndiyeno anawalangiza mwamphamvu kuti asauze aliyense zimenezo.+ 22 Kenako anati: “Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri. Iye adzakanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa,+ koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+
23 Kenako anauza onse kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha+ ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo* tsiku ndi tsiku ndi kunditsatira mosalekeza.+ 24 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine, adzaupulumutsa.+ 25 Kunena zoona, kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma iyeyo n’kudzivulaza kapena kutaya moyo wake?+ 26 Pakuti aliyense wochita manyazi ndi ine, komanso ndi mawu anga, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi akadzafika mu ulemerero wake, wa Atate wake ndi wa angelo oyera.+ 27 Koma ndikukuuzani ndithu, Pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona ufumu wa Mulungu.”+
28 Patapita masiku pafupifupi 8 chinenereni mawu amenewa, iye anatenga Petulo, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera nawo m’phiri kukapemphera.+ 29 Pamene anali kupemphera, maonekedwe+ a nkhope yake anasintha ndipo chovala chake chinaoneka choyera kwambiri ndi chonyezimira.+ 30 Ndiyeno panaonekanso anthu awiri akukambirana naye. Anthu amenewa anali Mose ndi Eliya.+ 31 Amenewa anaonekera ndi ulemerero ndipo anayamba kukambirana za mmene adzachokere m’dzikoli, ku Yerusalemu.*+ 32 Apa n’kuti Petulo ndi ena amene anali naye atatopa ndi tulo. Koma mmene anayeranso m’maso anaona ulemerero+ wake ndiponso amuna awiri ataima naye. 33 Tsopano pamene amenewa anali kulekana naye, Petulo anauza Yesu kuti:+ “Mlangizi, ndi bwino kuti ife tizikhala pano. Choncho timange mahema atatu, limodzi lanu, limodzi la Mose ndi lina la Eliya.” Koma iye sanali kuzindikira zimene anali kunena. 34 Pamene anali kunena zimenezi, kunachita mtambo ndipo unayamba kuwaphimba. Pamene mtambowo unali kuwakuta, anachita mantha.+ 35 Ndiyeno mawu+ anatuluka mumtambomo akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga, amene ndinam’sankha.+ Mumvereni.”+ 36 Pamene mawuwo anali kumveka, anaona kuti Yesu ali yekha.+ Koma iwo anakhala chete ndipo sanauze aliyense m’masiku amenewo chilichonse mwa zimene anaonazo.+
37 Tsiku lotsatira, atatsika m’phirimo, chikhamu cha anthu chinam’chingamira.+ 38 Pamenepo munthu wina anafuula kuchokera m’khamulo kuti: “Mphunzitsi, ndikukupemphani kuti mukaone mwana wanga wamwamuna, chifukwa ndi mmodzi yekhayo.+ 39 Mzimu umam’gwira, ndipo mwadzidzidzi amafuula, kenako umam’tsalimitsa kwinaku akuchita thovu. Mzimu+ umenewu umamuvulaza kwambiri ndipo suchoka msanga. 40 Ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse, koma alephera.”+ 41 Poyankha Yesu anati: “Inu a m’badwo+ wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo, kodi ndikhala nanube ndi kupitiriza kukupirirani mpaka liti? Bwera naye kuno mwana wakoyo.”+ 42 Koma ngakhale pamene anali kufika naye kwa iye, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kum’tsalimitsa mwamphamvu. Yesu anakalipira mzimu wonyansawo ndi kuchiritsa mnyamatayo. Kenako anamupereka kwa bambo ake.+ 43 Pamenepo, onse anadabwa ndi mphamvu zodabwitsa+ za Mulungu.
Tsopano onse adakali odabwa ndi zonse zimene anali kuchita, Yesu anauza ophunzira ake kuti: 44 “Mumvetse bwino mawu awa, pakuti Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu.”+ 45 Koma ophunzirawo sanamvetsebe tanthauzo la mawu amenewa. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo kuti asazindikire, ndipo anaopa kumufunsa za mawu amenewa.+
46 Kenako iwo anayamba kukhala ndi maganizo ofuna kudziwa amene ali wamkulu koposa pakati pawo.+ 47 Yesu podziwa zimene anali kuganiza mumtima mwawo, anatenga mwana wamng’ono, n’kumuimika pafupi ndi iye.+ 48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense wolandira mwana wamng’ono uyu m’dzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense wolandira ine walandiranso amene anandituma ine.+ Pakuti aliyense wokhala ngati wamng’ono+ pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.”+
49 Ndiyeno Yohane ananena kuti: “Mlangizi, tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda+ m’dzina lanu, choncho ife tinamuletsa+ chifukwa sakukutsatirani pamodzi ndi ife.”+ 50 Koma Yesu anamuuza kuti: “Musamuletse amuna inu, chifukwa amene sakutsutsana nanu ali kumbali yanu.”+
51 Pamene masiku oti akwere kumwamba+ anali kukwana, anatsimikiza mtima kupita ku Yerusalemu. 52 Choncho anatsogoza amithenga. Iwo ananyamuka ndi kukalowa m’mudzi wa Asamariya,+ kukakonzekera kufika kwake. 53 Koma iwo sanamulandire chifukwa mtima wake pa ulendowo unali ku Yerusalemu.+ 54 Ophunzira ake, Yakobo ndi Yohane,+ ataona zimenezi anati: “Ambuye, kodi mukufuna tiwaitanire moto+ kuchokera kumwamba kuti uwanyeketse?” 55 Koma iye anatembenuka ndi kuwadzudzula. 56 Choncho anapita kumudzi wina.
57 Tsopano ali pa ulendowo, winawake anauza Yesu kuti: “Ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.”+ 58 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.”+ 59 Kenako anauza munthu wina kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Koma munthuyo anati: “Ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.”+ 60 Yesu anamuyankha kuti: “Aleke akufa+ aike akufa awo, koma iwe pita kukalengeza ufumu wa Mulungu+ kwina kulikonse.” 61 Winanso ananena kuti: “Ine ndikutsatirani Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsanzika a m’banja langa.”+ 62 Yesu anamuuza kuti: “Aliyense wogwira pulawo+ koma n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo+ sayenera ufumu wa Mulungu.”
10 Pambuyo pake, Ambuye anasankha anthu ena 70+ ndi kuwatumiza awiriawiri+ kuti atsogole kupita mumzinda ndi malo alionse kumene iye adzafikeko. 2 Kenako anayamba kuwauza kuti: “Zokolola+ n’zochulukadi, koma antchito+ ndi ochepa. Choncho pemphani+ Mwini zokololazo kuti atumize antchito+ okam’kololera. 3 Pitani. Inetu ndikukutumizani monga nkhosa+ pakati pa mimbulu. 4 Musatenge chikwama cha ndalama, thumba la chakudya,+ kapena nsapato. Ndipo musamachedwe mukamapereka moni panjira.+ 5 Mukafika panyumba, choyamba muzinena kuti, ‘Mtendere ukhale panyumba pano.’+ 6 Ndipo ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendere, mtendere wanu udzakhala pa iye.+ Koma ngati palibe, udzabwerera kwa inu.+ 7 Choncho khalani m’nyumba yamtendereyo.+ Muzidya ndi kumwa zimene angakupatseni,+ chifukwa wantchito ayenera kulandira malipiro ake.+ Musamachoke kumene mwafikirako n’kupita kunyumba zina.+
8 “Komanso mukalowa mumzinda ndipo iwo n’kukulandirani, muzidya zimene akukonzerani. 9 Muzichiritsanso+ odwala mmenemo ndipo muziwauza kuti, ‘Ufumu wa Mulungu+ wakuyandikirani.’ 10 Koma mukalowa mumzinda ndipo sanakulandireni,+ muzichokamo ndi kupita m’misewu yawo n’kunena kuti, 11 ‘Ngakhale fumbi la mumzinda wanu uno, limene lamamatira kumapazi kwathu, tikukusansirani.+ Komabe, kumbukirani kuti, ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12 Ndithu ndikukuuzani, chilango cha Sodomu+ pa tsiku limenelo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha mzinda umenewo.
13 “Tsoka iwe Korazini!+ Tsoka iwe Betsaida!+ Chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika kumeneko zikanachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu kumeneko akanalapa kalekale atavala ziguduli n’kukhala paphulusa.+ 14 Choncho chilango cha Turo ndi Sidoni pa chiweruzo chidzakhala chocheperako kusiyana ndi chanu.+ 15 Iwenso Kaperenao, kodi udzakwezedwa kumwamba kapena?+ Ku Manda*+ n’kumene udzatsikira ndithu!
16 “Amene akukumverani,+ akumveranso ine. Ndipo amene akunyalanyaza+ inu akunyalanyazanso ine. Ndipotu amene akunyalanyaza ine akunyalanyazanso amene anandituma.”
17 Tsopano anthu okwana 70 aja anabwerera ali osangalala. Iwo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera+ pamene tinagwiritsa ntchito dzina lanu.” 18 Ndiyeno iye anawauza kuti: “Ndinayamba kuona Satana atagwa+ kale ngati mphezi kuchokera kumwamba. 19 Taonani! Inetu ndakupatsani ulamuliro kuti muzitha kupondaponda njoka+ ndi zinkhanira.+ Komanso ndakupatsani ulamuliro pa mphamvu zonse za mdani,+ ndipo palibe chimene chidzakuvulazeni. 20 Komano, musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina+ anu alembedwa kumwamba.” 21 Nthawi yomweyo Yesu anakondwera+ kwambiri mwa mzimu woyera n’kunena kuti: “Atate ndikukutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzeru+ ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana. Inde Atate, chifukwa inu munakonda kuti zinthu zikhale chonchi. 22 Atate wanga wapereka+ zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso Atatewo+ palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana+ yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.”
23 Ndiyeno Yesu ndi ophunzira akewo ali kwaokha, anawauza kuti: “Anthu amene maso awo amaona zimene inu mukuonazi ndi odala.+ 24 Pakuti ndikukuuzani, Aneneri ndi mafumu ambiri analakalaka kuona+ zimene mukuzionazi, koma sanazione. Analakalaka kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”
25 Kenako munthu wina wodziwa Chilamulo+ anaimirira kuti amuyese. Iye anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 26 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo analembamo chiyani?+ Umawerengamo zotani?” 27 Iye anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, mphamvu zako zonse, ndi maganizo ako onse.’+ Komanso, ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ 28 Pamenepo anamuuza kuti: “Wayankha molondola. ‘Uzichita zimenezo, ndipo udzapeza moyo.’”+
29 Koma pofuna kudzionetsa kuti ndi wolungama, munthuyo anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?”+ 30 Poyankha Yesu anati: “Munthu wina anali kuyenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Ndipo anakumana ndi achifwamba amene anam’vula ndi kumumenya koopsa. Kenako anapita, n’kumusiya ali pafupi kufa. 31 Ndiye zinangochitika kuti wansembe wina anali kuyenda mumsewu womwewo, koma atamuona, anangomulambalala.+ 32 Chimodzimodzinso Mlevi, atadutsa msewuwo n’kufika pamalo amenewo ndi kumuona, anangomulambalala.+ 33 Koma panafika Msamariya+ wina amene anali kudutsanso msewu umenewo. Ndipo atamuona, anagwidwa chifundo. 34 Choncho anam’yandikira ndi kumanga mabala ake. Anathira mafuta ndi vinyo m’mabalamo.+ Kenako anam’kweza pachiweto chake n’kupita naye kunyumba ya alendo kumene anam’samalira. 35 Tsiku lotsatira anatulutsa madinari awiri ndi kupereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Ndiyeno anamuuza kuti, ‘Musamalireni bwino, mukawononga ndalama zina zowonjezera, ndidzakubwezerani ndikadzabwera.’ 36 Ndani mwa atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakonda+ munthu amene anakumana ndi achifwambayu?” 37 Iye anayankha kuti: “Ndi amene anam’chitira chifundoyo.”+ Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.”+
38 Tsopano pamene anali kuyenda, analowa m’mudzi wina. Kumeneko mayi wina dzina lake Marita+ anamulandira m’nyumba mwake monga mlendo. 39 Mayi ameneyu anali ndi m’bale wake dzina lake Mariya. Iyeyu anakhala pansi pafupi+ ndi Ambuye n’kumamvetsera mawu awo. 40 Koma Marita anatanganidwa+ ndi ntchito zochuluka. Choncho anafika pafupi n’kunena kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekerera ndekha ntchito?+ Tamuuzani kuti andithandize.” 41 Poyankha Ambuye anamuuza kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa+ ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri.+ 42 Komatu zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa+ chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi. Kumbali yake, Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri,+ ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.”
11 Tsopano Yesu anali kupemphera pamalo enaake. Atatsiriza, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera,+ ngati mmene Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”+
2 Pamenepo iye anawauza kuti: “Mukamapemphera+ muzinena kuti, ‘Atate, dzina lanu liyeretsedwe.+ Ufumu wanu ubwere.+ 3 Mutipatse chakudya+ chathu chalero malinga ndi chakudya chofunika pa tsikuli. 4 Ndipo mutikhululukire machimo athu,+ pakuti nafenso timakhululukira aliyense amene amatilakwira.*+ Komanso musatilowetse m’mayesero.’”+
5 Kenako anawauza kuti: “Ndani wa inu amene ali ndi bwenzi lake kumene angapite pakati pa usiku kukam’pempha kuti, ‘Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate, 6 chifukwa mnzanga wangofika kumene kuchokera ku ulendo ndipo ndilibe chomupatsa’? 7 Ndiyeno ali m’nyumbayo n’kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine.+ Takhoma kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona kale. Sindingadzukenso kuti ndikupatse kanthu.’ 8 Ndithu ndikukuuzani, Adzadzuka ndi kum’patsa zonse zimene akufuna, osati chifukwa chakuti ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha kukakamira kwake.+ 9 Choncho ndikukuuzani, Pemphanibe,+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna,+ ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. 10 Pakuti aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzam’tsegulira. 11 Kodi kapena pakati panu alipo bambo amene mwana wake+ atam’pempha nsomba, angam’patse njoka m’malo mwa nsomba? 12 Kapena atam’pempha dzira iye angam’patse chinkhanira? 13 Choncho ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu+ mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera+ kwa amene akum’pempha.”
14 Nthawi inayake anali kutulutsa chiwanda cholepheretsa munthu kulankhula.+ Chiwandacho chitatuluka, munthu wosalankhulayo analankhula, ndipo khamu la anthu linadabwa kwambiri. 15 Koma ena mwa iwo anati: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule* wolamulira wa ziwanda.”+ 16 Koma ena pofuna kumuyesa, anayamba kumupempha kuti awasonyeze chizindikiro+ chochokera kumwamba. 17 Podziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha, ndipo nyumba yogawanika imagwa.+ 18 Choncho ngati Satana wagawanika, ufumu wake ungalimbe bwanji?+ Chifukwa inu mukuti ndikutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule. 19 Ngati ndikutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule, kodi otsatira anu+ akuzitulutsa ndi chiyani? Pa chifukwa chimenechi iwo adzakuweruzani. 20 Koma ngati ziwandazo ndikuzitulutsa ndi chala cha Mulungu,+ ndiye kuti ufumu wa Mulungu wakufikiranidi modzidzimutsa.+ 21 Munthu wamphamvu,+ wokhala ndi zida zokwanira, akamalondera nyumba yake, chuma chake chimatetezeka. 22 Koma wina wamphamvu kuposa iyeyu+ akabwera n’kumugonjetsa,+ amamulanda zida zake zonse zimene amadalira, ndipo katundu amene wamulanda, amamugawa kwa ena. 23 Amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine, ndipo amene sasonkhanitsa anthu pamodzi ndi ine amawabalalitsa.+
24 “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo ouma kufunafuna malo okhala, koma akapanda kupezeka, umanena kuti, ‘Ndibwerera m’nyumba yanga mmene ndinatuluka muja.’+ 25 Tsopano ukafikamo umapeza muli mosesa bwino komanso mokongola. 26 Kenako umapita kukatenga mizimu ina 7+ yoipa kwambiri kuposa umenewu, ndipo ikalowa mkatimo, imakhala mmenemo. Potsirizira pake zochita za munthu ameneyu zimakhala zoipa kwambiri kuposa poyamba paja.”+
27 Pamene anali kunena mawu amenewa, mayi wina m’khamu la anthulo anafuula n’kumuuza kuti: “Ndi wodala mayi+ amene mimba yake inanyamula inu ndiponso amene munayamwa mabere ake!” 28 Koma iye anati: “Ayi, m’malomwake, Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”+
29 Pamene anthu osonkhana pamodzi anali kuchulukirachulukira, iye anayamba kunena kuti: “M’badwo uwu ndi m’badwo woipa, ukufuna chizindikiro.+ Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.+ 30 Monga momwe Yona+ anakhalira chizindikiro kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu adzakhalanso chizindikiro ku m’badwo uwu. 31 Mfumukazi+ ya kum’mwera adzaiimiritsa pa chiweruzo limodzi ndi anthu a m’badwo uwu, ndipo idzawatsutsa. Chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa+ Solomo ali pano. 32 Anthu a ku Nineve adzaimirira pa chiweruzo limodzi ndi m’badwo uwu ndipo adzautsutsa. Chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa+ Yona ali pano. 33 Munthu akayatsa nyale saiika m’chipinda cha pansi kapena kuivundikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale,+ kuti onse olowa aone kuwala. 34 Nyale ya thupi ndi diso lako. Ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi, thupi lako lonse limawala kwambiri.+ Koma ngati lili loipa, thupi lako limachita mdima. 35 Chotero khala tcheru. Mwina kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima.+ 36 Choncho ngati thupi lako lonse lili lowala kwambiri, popanda mbali ina yamdima, thupi lonse lidzawala kwambiri+ ngati mmene nyale imachitira pokuunikira ndi kuwala kwake.”
37 Atalankhula zimenezi, Mfarisi wina anam’pempha kuti akadye naye.+ Choncho iye anapitadi kukadya chakudya. 38 Koma Mfarisiyo anadabwa kuona kuti anayamba kudya chakudyacho asanasambe.+ 39 Choncho Ambuye anamuuza kuti: “Inu Afarisi mumayeretsa kunja kwa kapu ndi mbale, koma mkati+ mwanu mwadzaza maganizo ofuna kulanda zinthu za anthu ndi kuchita zinthu zoipa.+ 40 Anthu opanda nzeru inu! Amene anapanga kunja+ anapanganso mkati, si choncho kodi? 41 Koma inu, perekani zimene zili mkati monga mphatso zachifundo,+ mukatero zina zonse zokhudza inuyo zidzakhala zoyera. 42 Tsoka inu Afarisi, chifukwa mumapereka chakhumi+ cha timbewu ta minti ndi ta luwe, ndi cha mbewu zakudimba zamtundu uliwonse. Koma mumanyalanyaza chilungamo ndi chikondi cha Mulungu! Unalidi udindo wanu kuchita zinthu zimenezi, koma simunayenera kusiya zinazo.+ 43 Tsoka inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yakutsogolo m’masunagoge ndi kupatsidwa moni m’misika!+ 44 Tsoka inu, chifukwa muli ngati manda achikumbutso osaonekera, moti anthu amayenda pamwamba pake koma osadziwa!”+
45 Poyankha wina wodziwa+ Chilamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, izi mukunenazi mukunyoza ndi ife tomwe.” 46 Pamenepo iye anati: “Tsoka inunso odziwa Chilamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wovuta kunyamula, koma inuyo simukhudza katunduyo ngakhale ndi chala chokha!+
47 “Tsoka inu, chifukwa mumamanga manda achikumbutso a aneneri, komatu makolo anu ndi amene anawapha!+ 48 Mosakayikira, ndinu mboni pa zimene makolo anu anachita. Ndipo mukugwirizana+ nawonso, chifukwa iwo anapha+ aneneri, pamene inu mukumanga manda awo. 49 Pa nkhani imeneyi, nzeru+ ya Mulungu inanenanso kuti, ‘Ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, koma iwo adzapha ndi kuzunza ena mwa iwo. 50 N’chifukwa chake m’badwo uwu udzafunsidwa za magazi a aneneri,+ okhetsedwa kuchokera pamene dziko linakhazikika.+ 51 Kuyambira magazi a Abele+ mpaka magazi a Zekariya,+ amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi nyumba yopatulika.’+ Inde, ndikukuuzani, m’badwo uwu udzafunsidwa za magazi amenewo.
52 “Tsoka inu odziwa Chilamulo, chifukwa munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziwa zinthu.+ Inuyo simunalowemo, ndipo ofuna kulowamo munawatsekereza!”+
53 Choncho atachoka kumeneko, alembi ndi Afarisi anayamba kumuunjirira koopsa ndi kum’panikiza ndi mafunso okhudza zinthu zina. 54 Anali kuyembekezera+ kumva mawu oti amutape nawo m’kamwa.+
12 Pa nthawiyi, chikhamu cha anthu masauzandemasauzande chinali chitasonkhana, moti anali kupondanapondana. Pamenepo Yesu anayamba kulankhula ndi ophunzira ake choyamba kuti: “Samalani ndi chofufumitsa+ cha Afarisi, chimene chili chinyengo.+ 2 Komatu palibe chobisika chimene sichidzaululika, ndi chinsinsi chimene sichidzadziwika.+ 3 Choncho zimene mumanena mumdima zidzamveka poyera, zimene mumanong’ona kwanokha m’zipinda zanu zidzalalikidwa pamadenga.+ 4 Komanso ndikukuuzani ndithu, mabwenzi anga,+ Musamaope amene amapha thupi lokha, amene sangathe kuchita zoposa pamenepa.+ 5 Koma ndikuuzani woti muzimuopa: Muziopa iye+ amene amati akapha, amakhalanso ndi mphamvu zoponya munthu m’Gehena.*+ Ndithu ndikukuuzani, muziopa+ Ameneyu. 6 Mpheta zisanu amazigulitsa makobidi awiri ochepa mphamvu, si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imene imaiwalika kwa Mulungu.+ 7 Ndipo ngakhale tsitsi+ lonse la m’mutu mwanu analiwerenga. Musachite mantha. Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.+
8 “Chotero ndikukuuzani kuti, Aliyense wovomereza+ pamaso pa anthu kuti ali kumbali yanga, Mwana wa munthunso adzavomereza pamaso pa angelo a Mulungu kuti ali kumbali yake.+ 9 Koma aliyense wondikana+ ine pamaso pa anthu, adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.+ 10 Ndipo aliyense wonena mawu onyoza Mwana wa munthu, adzakhululukidwa. Koma wonyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa.+ 11 Akapita nanu kumabwalo amilandu, ndi kwa akuluakulu aboma, komanso kwa olamulira, musade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukanena chiyani.+ 12 Pakuti mzimu woyera+ udzakuphunzitsani mu ola lomwelo zoyenera kunena.”+
13 Kenako wina mukhamulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mundiuzireko m’bale wanga kuti andigawireko cholowa.” 14 Iye anamuuza kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika ine kukhala woweruza+ kapena wogawa chuma chanu?” 15 Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”+ 16 Atatero anawauza fanizo, kuti: “Munda wa munthu wina wachuma unabereka bwino. 17 Choncho anayamba kudzifunsa kuti, ‘Ndichite chiyani tsopano, popeza ndilibe mosungira zokolola zangazi?’ 18 Ndiyeno anati, ‘Ndichita izi:+ Ndipasula nkhokwe zanga ndi kumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse zabwino ndidzazitutira mmenemo.+ 19 Ndipo ndidzauza+ moyo wanga kuti: “Moyo wangawe, uli ndi zinthu zambiri zabwino mwakuti zisungika kwa zaka zambiri. Ungoti phee tsopano, ndipo udye, umwe ndi kusangalala.”’+ 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+ 21 Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”+
22 Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Pa chifukwa chimenechi ndikukuuzani kuti, Lekani kudera nkhawa moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena kudera nkhawa matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ 23 Pakuti moyo ndi wofunika kwambiri kuposa chakudya, ndipo thupi ndi lofunika kwambiri kuposa chovala. 24 Onetsetsani makwangwala,+ iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nyumba yosungiramo zinthu kapena nkhokwe, komatu Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ofunika kwambiri kuposa mbalame?+ 25 Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa?+ 26 Choncho ngati inu simungachite kanthu kochepaka, n’kuderanji nkhawa+ ndi zinthu zinazo? 27 Onetsetsani mmene maluwa amakulira.+ Iwo sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. Koma ndikukuuzani, Ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati duwa lililonse mwa maluwa amenewa.+ 28 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo.+ 29 Choncho lekani kudera nkhawa za chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa, ndipo siyani kuvutika mumtima.+ 30 Pakuti zonsezi ndi zinthu zimene anthu a mitundu ina a m’dzikoli amazifunafuna mwakhama, koma Atate wanu amadziwa kuti zinthu zonsezi n’zofunika kwa inu.+ 31 Koma inu, pitirizani kufunafuna ufumu wake, ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.+
32 “Musaope,+ kagulu ka nkhosa+ inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.+ 33 Gulitsani+ zinthu zanu ndi kupereka mphatso zachifundo.+ Dzipangireni zikwama za ndalama zomwe sizingathe, kutanthauza chuma chosatha kumwamba,+ kumene mbala singafikeko, ndipo njenjete* singawononge. 34 Pakuti kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko.+
35 “Mangani m’chiuno mwanu+ ndipo nyale+ zanu zikhale chiyakire. 36 Inuyo mukhale ngati anthu amene akuyembekezera kubwera kwa mbuye wawo+ kuchokera ku ukwati,+ kuti akafika ndi kugogoda+ amutsegulire mwamsanga. 37 Odala ndi akapolo amene mbuye wawo pofika adzawapeza akudikira!+ Ndithu ndikukuuzani, Iye adzamanga m’chiuno+ mwake ndi kuwakhazika patebulo kuti adye chakudya ndipo adzawatumikira.+ 38 Iwo ndi odala ndithu ngati atawapeza akudikirabe ngakhale atafika pa ulonda wachiwiri kapenanso wachitatu!*+ 39 Koma dziwani kuti mwininyumba atadziwa nthawi yobwera mbala, angakhale maso ndipo sangalole kuti mbala zithyole ndi kulowa m’nyumba mwake.+ 40 Inunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.”+
41 Kenako Petulo anati: “Ambuye, kodi mukunena fanizoli kwa ife tokha kapenanso kwa ena onse?” 42 Pamenepo Ambuye ananena kuti: “Ndani kwenikweni amene ali mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika+ ndi wanzeru,+ amene mbuye wake adzamuika kuyang’anira gulu la atumiki ake, kuti aziwapatsa chakudya chokwanira pa nthawi yake?+ 43 Kapolo ameneyo ndi wodala, ngati mbuye wake pobwera adzam’peze akuchita zimenezo!+ 44 Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kukhala woyang’anira zinthu zake zonse.+ 45 Koma ngati kapoloyo anganene mumtima mwake kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’+ Ndiyeno n’kuyamba kumenya antchito anzake aamuna ndi aakazi, kudya, kumwa ndi kuledzera,+ 46 mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera, ndi pa ola limene sakulidziwa,+ ndipo adzam’patsa chilango choopsa ndi kum’patsa gawo pamodzi ndi anthu osakhulupirika.+ 47 Pa nthawiyo kapolo amene anadziwa zofuna za mbuye wake koma osakonzekera kubwera kwake, kapena osachita mogwirizana ndi zofuna za mbuye wakeyo, adzakwapulidwa zikoti zambiri.+ 48 Koma amene sanadziwe+ ndipo wachita zinthu zofunika kum’kwapula zikoti, adzam’kwapula zikoti zochepa.+ Inde, aliyense amene anapatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunika kwa iye.+ Ndipo aliyense amene anthu anamuika kuyang’anira zinthu zochuluka, anthuwo adzafunanso zochuluka kwa iye.+
49 “Ndinabwera kudzakoleza moto+ padziko lapansi, ndiye ngati motowo wayaka kale, chinanso n’chiyani chimene ndingafune? 50 Ndithudi pali ubatizo umene ndiyenera kubatizidwa nawo, ndipotu ndikuvutika kwambiri mumtima kufikira utatha!+ 51 Kodi mukuganiza kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi? Ayi ndithu, koma ndinabwera kudzagawanitsa anthu.+ 52 Pakuti kuyambira tsopano, m’nyumba imodzi mudzakhala anthu asanu osemphana maganizo, atatu kutsutsana ndi awiri, awiri kutsutsana ndi atatu.+ 53 Iwo adzagawanika, bambo kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna, ndipo mwana wamwamuna kutsutsana ndi bambo ake. Mayi kutsutsana ndi mwana wake wamkazi, ndipo mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake. Mpongozi kutsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndipo mkazi wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.”+
54 Kenako anauzanso khamu la anthulo kuti: “Mukaona mtambo ukukwera chakumadzulo, nthawi yomweyo mumanena kuti, ‘Kukubwera chimvula,’ ndipo chimabweradi.+ 55 Ndipo mukaona mphepo ya kum’mwera ikuwomba, mumanena kuti, ‘Lero kutentha kwambiri,’ ndipo zimachitikadi. 56 Onyenga inu! Mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi kuthambo. Nanga zimakukanikani bwanji kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika pa nthawi ino?+ 57 N’chifukwa chiyani inuyo panokha simuzindikira chimene chili cholungama?+ 58 Mwachitsanzo, pamene wokusumira mlandu akupita nawe kwa wolamulira, yesetsa kuchitapo kanthu muli m’njira, kuti uthetse mlanduwo. Uchitepo kanthu kuti asakutengere kwa woweruza, ndi kutinso woweruzayo asakupereke kwa msilikali wa pakhoti, ndipo msilikaliyo n’kukuponya m’ndende.+ 59 Ndithu ndikukuuza, Sudzatulukamo kufikira utapereka kakhobidi kotsiriza kochepa mphamvu kwambiri.”+
13 Pa nthawiyo, panali anthu ena amene anam’fotokozera za Agalileya+ amene magazi awo, Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo. 2 Choncho poyankha iye anawauza kuti: “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewo anali ochimwa kwambiri+ kuposa Agalileya ena onse chifukwa chakuti zimenezo zinawachitikira? 3 Ndithudi ayi. Choncho ndikukuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzawonongeka mofanana ndi iwowo.+ 4 Nanga bwanji za anthu 18 aja, amene nsanja inawagwera ku Siloamu n’kuwapha? Kodi mukuganiza kuti iwo anali ochimwa kwambiri kuposa anthu onse okhala mu Yerusalemu? 5 Ndithudi ayi. Choncho ndikukuuzani kuti, ngati simulapa, nonsenu mudzawonongeka ngati mmene iwo anawonongekera.”+
6 Kenako anayamba kufotokoza fanizo ili: “Munthu wina anali ndi mkuyu m’munda wake wa mpesa,+ ndipo anapita kukafuna chipatso mumtengowo,+ koma sanapezemo chilichonse.+ 7 Ndiyeno anauza munthu wosamalira munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu+ tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna nkhuyu mumtengo uwu, koma sindinapezemo ngakhale imodzi. Dula mtengo umenewu!+ N’chifukwa chiyani ukungowononga nthaka?’ 8 Wosamalira mundayo anayankha kuti, ‘Mbuyanga, bwanji muusiye+ chaka chino chokha. Ine ndikumba mouzungulira n’kuthirapo manyowa. 9 Ukadzabala zipatso m’tsogolo, zidzakhala bwino, koma ngati sudzabala mudzaudule.’”+
10 Tsopano anali kuphunzitsa m’sunagoge winawake pa sabata. 11 Mmenemo munali mayi wina amene mzimu+ woipa unamudwalitsa zaka 18. Anali wopindika msana moti sankatha kuweramuka. 12 Yesu atamuona, anamulankhula kuti: “Mayi, mwamasuka+ ku matenda anu.” 13 Pamenepo anaika manja ake pamayiyo, ndipo nthawi yomweyo anaweramuka,+ n’kuyamba kutamanda Mulungu. 14 Koma mtsogoleri wa sunagoge ataona izi, anakwiya chifukwa Yesu anachiritsa munthu pa sabata.+ Choncho anayamba kuuza khamu la anthu kuti: “Pali masiku 6 oyenera kugwira ntchito. Muzibwera masiku amenewo kudzachiritsidwa, osati tsiku la sabata.”+ 15 Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Onyenga inu,+ kodi aliyense wa inu samasula ng’ombe yake kapena bulu wake m’khola pa sabata ndi kupita naye kukam’mwetsa madzi?+ 16 Kodi sikunali koyenera kuti mayi uyu, amenenso ndi mwana wa Abulahamu,+ amene Satana anamumanga zaka 18, amasulidwe m’maunyolo amenewa tsiku la sabata?” 17 Atanena zimenezi, onse omutsutsa anachita manyazi.+ Koma khamu lonse la anthu linayamba kukondwera ndi zodabwitsa zonse zimene iye anachita.+
18 Pamenepo anapitiriza kuti: “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndiuyerekeze ndi chiyani?+ 19 Uli ngati kanjere ka mpiru,* kamene munthu anakatenga ndi kukaponya m’munda wake. Kenako kanamera ndi kukhala mtengo, moti mbalame zam’mlengalenga+ zinapeza malo okhala m’nthambi zake.”+
20 Iye ananenanso kuti: “Kodi ufumu wa Mulungu ndiuyerekeze ndi chiyani? 21 Uli ngati chofufumitsa chimene mayi wina anachitenga ndi kuchibisa mu ufa wokwana mbale zoyezera zazikulu zitatu, moti mtanda wonsewo unafufuma.”+
22 Yesu anayenda mumzinda ndi mzinda, komanso mudzi ndi mudzi. Anali kuphunzitsa ndi kupitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu.+ 23 Tsopano munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi amene akupulumuka ndi owerengeka okha?”+ Iye anawauza kuti: 24 “Yesetsani+ mwamphamvu kulowa pakhomo lopapatiza.+ Chifukwa ambiri ndikukuuzani, adzafunitsitsa kulowamo koma sadzatha.+ 25 Mwininyumba akanyamuka ndi kukakhoma chitseko, ndiyeno inu n’kuima panja ndi kuyamba kugogoda pachitsekopo, n’kumanena kuti, ‘Titsegulireni ambuye,’+ iye poyankha adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera.’+ 26 Pamenepo mudzayamba kunena kuti, ‘Tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo inu munaphunzitsa m’misewu yathu.’+ 27 Koma iye adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera. Ndichokereni pano, nonsenu ochita zinthu zosalungama!’+ 28 Kunjako n’kumene inu mudzalira ndi kukukuta mano,+ pamene mudzaona Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, komanso aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu,+ koma inuyo atakukankhirani kunja. 29 Komanso, anthu adzabwera kuchokera kumbali za kum’mawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera,+ ndipo adzadya patebulo mu ufumu wa Mulungu.+ 30 Ndithudi amene ali omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.”+
31 Mu ola lomwelo kunafika Afarisi ena ndi kumuuza kuti: “Nyamukani muchoke kuno, chifukwa Herode* akufuna kukuphani.” 32 Iye anawayankha kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe+ imeneyo kuti, ‘Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchita ntchito yochiritsa lero ndi mawa, tsiku lachitatu ndidzamaliza.’+ 33 Komabe ndiyenera kupitiriza ulendo wanga lero ndi mawa ndi tsiku linalo, chifukwa n’kosayenera kuti mneneri amuphere kunja kwa Yerusalemu.+ 34 Yerusalemu, Yerusalemu! wakupha+ aneneri ndi kuponya miyala+ anthu otumidwa kwa iwe . . . mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako monga mmene nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko ake,+ koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 35 Tsopano tamverani! Mulungu wachoka ndi kukusiyirani nyumba* yanuyi.+ Ndithu ndikukuuzani, simudzandionanso kufikira pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!’”+
14 Kanthawi kena atalowa m’nyumba ya mmodzi wa akuluakulu a Afarisi pa sabata kukadya chakudya,+ Afarisiwo anali kumuyang’anitsitsa.+ 2 Patsogolo pake panakhala munthu amene anali kudwala matenda amene anamutupitsa manja ndi miyendo. 3 Atamuona, Yesu analankhula ndi odziwa Chilamulo ndi Afarisiwo kuti: “Kodi n’kololeka kuchiritsa pa sabata kapena ayi?”+ 4 Koma iwo anangokhala chete. Pamenepo iye anagwira munthu uja, n’kumuchiritsa ndi kumuuza kuti azipita kwawo. 5 Ndiyeno anawauza kuti: “Ndani wa inu, amene mwana wake kapena ng’ombe yake itagwera m’chitsime+ pa tsiku la sabata, sangaitulutse nthawi yomweyo?”+ 6 Iwo sanathe kumuyankha pa zinthu zimenezi.+
7 Ataona mmene anthu oitanidwawo anali kusankhira malo olemekezeka kwambiri, anawauza fanizo kuti:+ 8 “Wina akakuitana kuphwando laukwati, usakhale pamalo olemekezeka kwambiri.+ Mwina n’kutheka kuti waitananso wina wolemekezeka kuposa iwe, 9 ndipo amene wakuitana uja angabwere ndi wolemekezekayo kudzakuuza kuti, ‘Choka pamenepa pakhale bambo awa.’ Pamenepo udzachokapo mwamanyazi n’kukakhala kumapeto kwenikweni.+ 10 Koma ukaitanidwa, pita ndipo ukakhale kumapeto kwenikweni,+ kuti munthu amene wakuitana uja akafika adzakuuze kuti, ‘Bwanawe, khala pamalo aulemuwa.’ Pamenepo udzalemekezeka pamaso pa alendo anzako onse.+ 11 Pakuti aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”+
12 Kenako anauzanso munthu amene anamuitana uja kuti: “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usaitane mabwenzi ako, kapena abale ako, kapena afuko lako, kapena anthu olemera omwe amakhala nawe pafupi. Mwina nthawi ina iwonso angadzakuitane ndipo kudzakhala ngati kukubwezera. 13 Koma ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu.+ 14 Ukatero udzakhala wodala, chifukwa alibe choti adzabweze kwa iwe. Pakuti udzabwezeredwa pa kuuka+ kwa anthu olungama.”
15 Atamva izi, mmodzi wa alendo anzake anamuuza kuti: “Wodala ndi munthu wakudya chakudya mu ufumu wa Mulungu.”+
16 Yesu anamuuza kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la chakudya chamadzulo ndipo anaitana anthu ambiri.+ 17 Nthawi ya chakudya chamadzulocho itakwana, anatumiza kapolo wake kukauza oitanidwawo kuti, ‘Tiyeni,+ chifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’ 18 Koma onse mofanana anayamba kupereka zifukwa zokanira.+ Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndagula munda, choncho ndiyenera kupita kukauona. Pepani sinditha kufika!’+ 19 Wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ng’ombe 10 zapagoli ndipo ndikupita kukaziyesa. Pepani sinditha kufika!’+ 20 Komanso wina anati, ‘Ine ndangokwatira kumene,+ choncho sindingathe kubwera.’ 21 Ndiyeno kapolo uja anabwerera kukanena zimenezi kwa mbuye wake. Pamenepo mwininyumba anakwiya ndi kuuza kapolo wake kuti, ‘Pita mwamsanga m’misewu ndi m’njira za mumzindawu, ukatenge anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi olumala ndi kubwera nawo kuno.’+ 22 Patapita kanthawi kapolo uja anati, ‘Mbuyanga, zimene munalamula zachitika, komabe malo adakalipo.’ 23 Ndiyeno mbuye uja anauza kapolo wakeyo kuti, ‘Pita m’misewu+ ndi malo a kumpanda, uwalimbikitse kuti abwere kuno kuti nyumba yanga idzaze.+ 24 Pakuti ndikukuuzani anthu inu, Palibe ndi mmodzi yemwe mwa oitanidwa aja amene adzalaweko chakudya changa chamadzulochi.’”+
25 Tsopano khamu lalikulu la anthu linali kuyenda limodzi ndi Yesu. Kenako anacheuka ndi kuwauza kuti: 26 “Ngati wina wabwera kwa ine, koma osadana ndi bambo ake, mayi ake, mkazi wake, ana ake, abale ake ndi alongo ake, ngakhale moyo wake umene,+ sangakhale wophunzira wanga.+ 27 Aliyense wosanyamula mtengo wake wozunzikirapo* ndi kunditsatira ine sangakhale wophunzira wanga.+ 28 Mwachitsanzo, ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge,+ kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo? 29 Akapanda kutero, angayale maziko koma osatha kuimaliza, ndipo onse oona angayambe kumuseka, 30 n’kumanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma zamukanika kumaliza.’ 31 Kapena ndi mfumu yanji, imene popita kukakumana ndi mfumu inzake pa nkhondo, siyamba yakhala pansi ndi kuganiza mofatsa ngati asilikali ake 10,000 angathe kulimbana ndi asilikali 20,000 a mfumu yobwera kudzalimbana naye?+ 32 Koma akaona kuti sangakwanitse, mwamsanga amatumiza akazembe kwa mfumu inayo isanafike pafupi, kukapempha mtendere.+ 33 Choncho, dziwani ichi, ndithu palibe aliyense wolephera kulekana ndi chuma chake chonse+ amene angathe kukhala wophunzira wanga.
34 “Kunena zoona, mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, kodi mphamvu yake ingabwezeretsedwe bwanji?+ 35 Ndi wosayeneranso ngakhale kuuthira m’nthaka kapena m’manyowa. Anthu amangoutaya kunja. Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+
15 Tsopano okhometsa msonkho+ komanso anthu ochimwa,+ onse anali kubwera kwa iye kudzamumvetsera. 2 Afarisi ndi alembi ataona zimenezi anayamba kung’ung’udza kuti: “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa ndi kudya nawo limodzi.”+ 3 Pamenepo anawauza fanizo ili: 4 “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi n’kutayika, sangasiye nkhosa 99 zinazo m’chipululu, n’kupita kukafunafuna imodzi yotayikayo kufikira ataipeza?+ 5 Ndipotu akaipeza amainyamula paphewa pake ndipo amakondwera.+ 6 Akafika kunyumba amasonkhanitsa mabwenzi ake ndi anthu oyandikana naye n’kuwauza kuti, ‘Kondwerani nane limodzi, chifukwa ndapeza nkhosa yanga imene inatayika ija.’+ 7 Ndithu ndikukuuzani, kumwamba kudzakhalanso chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa+ kuposa cha anthu 99 olungama osafunika kulapa.+
8 “Kapena ndi mayi uti amene atakhala ndi ndalama zokwana madalakima 10, imodzi n’kumutayika, sangayatse nyale ndi kusesa m’nyumba n’kuifufuza mosamala mpaka ataipeza? 9 Ndipo akaipeza amasonkhanitsa amayi ena amene ndi mabwenzi ake ndi oyandikana nawo, n’kuwauza kuti, ‘Kondwerani nane limodzi, chifukwa ndapeza khobidi la dalakima linanditayika lija.’ 10 Choncho ndikukuuzani, kumakhala chisangalalo chochuluka kwa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa.”+
11 Kenako ananena kuti: “Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri.+ 12 Wamng’ono pa awiriwo anapempha bambo ake kuti, ‘Bambo, mundipatsiretu cholowa changa pa chuma chanuchi.’+ Pamenepo bamboyo anagawa chuma chakecho+ kwa anawo. 13 Patangopita masiku owerengeka, mwana wamng’ono uja anasonkhanitsa zinthu zonse n’kupita kudziko lina lakutali. Kumeneko anasakaza chuma chake chonse mwa kulowerera m’makhalidwe oipa.+ 14 Atawononga zonse, m’dziko lonselo munagwa njala yaikulu, ndipo iye anayamba kuvutika kwambiri. 15 Moti anapita kukadziphatika kwa nzika ina ya m’dzikolo, ndipo anam’tumiza kubusa kwake kuti azikaweta nkhumba.+ 16 Iye anafika pomalakalaka chakudya cha nkhumbazo, ndipo palibe amene anali kum’patsa kanthu.+
17 “Nzeru zitam’bwerera, anati, ‘Komatu aganyu ambiri a bambo ali ndi chakudya chochuluka, koma ine kuno ndikufa ndi njala! 18 Basi ndinyamuka ndizipita+ kwa bambo anga ndikawauze kuti: “Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu.+ 19 Sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.”’ 20 Choncho ananyamukadi n’kupita kwa bambo ake. Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa chifundo. Pamenepo anamuthamangira ndi kumukumbatira ndipo anamupsompsona mwachikondi. 21 Ndiyeno mwanayo anauza bambo akewo kuti, ‘Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu.+ Sindilinso woyenera kutchedwa mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.’+ 22 Koma bambowo anauza akapolo ake kuti, ‘Fulumirani, tengani mkanjo wabwino kwambiri uja mumuveke!+ Mumuvekenso mphete+ kudzanja lake ndi nsapato kumapazi kwake. 23 Mubweretse mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa,+ mumuphe ndipo tidye tisangalale. 24 Chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa koma tsopano wakhalanso ndi moyo,+ anatayika koma wapezeka.’ Chotero onse anayamba kukondwerera.
25 “Koma mwana wamkulu+ anali kumunda. Ndiyeno pobwerako, atayandikira kunyumbako, anamva anthu akuimba nyimbo ndi kuvina. 26 Choncho anaitana mmodzi wa antchito ndi kumufunsa chimene chinali kuchitika. 27 Iye anamuuza kuti, ‘Mng’ono wanu+ wabwera, ndipo bambo anu+ amuphera mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa, chifukwa amulandira ali bwinobwino.’ 28 Pamenepo iye anakwiya kwambiri moti sanafune n’komwe kulowamo. Kenako bambo akewo anatuluka ndi kuyamba kumuchonderera.+ 29 Poyankha iye anauza bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ngati kapolo, ndipo sindinaphwanyepo malamulo anu n’kamodzi komwe, koma simunandipatseko ngakhale kamwana ka mbuzi kuti ndisangalale ndi mabwenzi anga.+ 30 Koma atangofika mwana wanuyu,+ amene anadya chuma chanu ndi mahule,+ mwamuphera mwana wa ng’ombe wamphongo wonenepa bwino.’+ 31 Pamenepo bambowo anauza mwanayo kuti, ‘Mwana wanga, iwe wakhala nane nthawi zonse, ndipo zinthu zonse zimene ine ndili nazo ndi zako.+ 32 Komatu sitikanachitira mwina, tinayeneradi kusangalala ndi kukondwera, chifukwa m’bale wakoyu anali wakufa koma tsopano ali ndi moyo, anali wotayika koma tsopano wapezeka.’”+
16 Kenako anauzanso ophunzira ake kuti: “Munthu wina anali wolemera ndipo anali ndi mtumiki woyang’anira nyumba+ yake. Mtumiki ameneyu ena anamuneneza kwa bwana wakeyo kuti anali kumusakazira chuma.+ 2 Choncho anamuitana ndi kumuuza kuti, ‘Ndamva zoipa zimene ukuchita. Pita ukalembe lipoti la mmene wagwirira ntchito yoyang’anira nyumba ino udzandipatse,+ pakuti supitiriza kuyendetsa ntchito za panyumba pano.’ 3 Pamenepo mtumikiyo mumtima mwake anati, ‘Nditani ine, pakuti bwana wanga+ andichotsa ntchito? Sindingathe kulima chifukwa ndilibe mphamvu, ndipo ndikuchita manyazi kukhala wopemphapempha. 4 Eya! Ndadziwa chochita kuti akandichotsa ntchito, anthu akandilandire bwino m’nyumba zawo.’+ 5 Ndiyeno anaitana amene anali ndi ngongole kwa bwana wake mmodzi ndi mmodzi, ndipo anafunsa woyamba kuti, ‘Uli ndi ngongole yochuluka bwanji kwa bwana wanga?’ 6 Iye anayankha kuti, ‘Mitsuko 100 ya mafuta a maolivi.’ Iye anamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako ya ngongole, khala pansi ulembe mitsuko 50 mwamsanga.’ 7 Kenako anafunsa wina kuti, ‘Nanga iwe, ngongole yako ndi yaikulu bwanji?’ Iye anayankha kuti, ‘Madengu 100 a tirigu.’ Iye anamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako ya ngongole ulembepo madengu 80.’ 8 Bwana wake uja anamuyamikira mtumiki ameneyu, ngakhale kuti anali wosalungama, chifukwa anachita mwanzeru.+ Pakuti ana a m’dziko lino amachita mwanzeru pochita zinthu ndi anthu a m’badwo wawo kuposa ana a kuwala.+
9 “Nanunso ndikukuuzani kuti, Dzipezereni mabwenzi+ ndi chuma chosalungama,+ kuti chumacho chikatha, akakulandireni m’malo okhala amuyaya.+ 10 Munthu wokhulupirika pa chinthu chaching’ono alinso wokhulupirika pa chinthu chachikulu, ndipo munthu wosalungama pa chinthu chaching’ono alinso wosalungama pa chinthu chachikulu.+ 11 Choncho, ngati simunakhale wokhulupirika pa chuma chosalungama, ndani adzakupatseni ntchito yoyang’anira chuma chenicheni?+ 12 Komanso ngati simunakhale wokhulupirika pa zinthu za ena,+ ndani adzakupatseni mphoto imene anakusungirani? 13 Wantchito wa panyumba sangatumikire ambuye awiri, chifukwa adzadana ndi mmodzi ndi kukonda wina, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”+
14 Tsopano Afarisi, amene anali okonda kwambiri ndalama, anali kumvetsera zonsezi, ndipo anayamba kumunyogodola.+ 15 Pamenepo iye anawauza kuti: “Inu mumadzitcha olungama pamaso pa anthu,+ koma Mulungu akudziwa mitima yanu.+ Chifukwa chimene chili chapamwamba kwa anthu n’chonyansa m’maso mwa Mulungu.+
16 “Anthu anali kulalikira Chilamulo ndi Zolemba za aneneri kudzafika m’nthawi ya Yohane.+ Kuchokera nthawi imeneyo, uthenga wabwino umene ukulengezedwa ndi wokhudza ufumu wa Mulungu, ndipo anthu osiyanasiyana akuyesetsa mwakhama kuti akalowemo.+ 17 Ndithudi, n’chapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke+ kusiyana n’kuti ngakhale mbali chabe ya chilembo chimodzi+ cha m’Chilamulo isakwaniritsidwe.+
18 “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo, ndipo wokwatira mkazi wosiyidwayo wachita chigololo.+
19 “Munthu winawake+ anali wolemera, ndipo nthawi zonse anali kuvala zovala zofiirira zapamwamba ndi nsalu zabwino kwambiri. Iye anali kusangalala ndi kudyerera tsiku ndi tsiku.+ 20 Koma munthu wina wopemphapempha dzina lake Lazaro, anali kumukhazika pachipata cha wachumayo, ali ndi zilonda thupi lonse. 21 Iyeyo ankalakalaka kudya nyenyeswa zakugwa patebulo la wachuma uja. Agalu nawonso anali kubwera kudzanyambita zilonda zakezo. 22 Patapita nthawi wopemphapempha uja anamwalira+ ndipo angelo anamutenga kukamuika pachifuwa+ cha Abulahamu.+
“Munthu wachuma ujanso anamwalira+ ndipo anaikidwa m’manda. 23 Ali m’Mandamo anakweza maso ake, ali mkati mozunzika,+ ndipo anaona Abulahamu kutali, ndipo Lazaro anali pachifuwa chake. 24 Choncho anaitana kuti, ‘Atate Abulahamu,+ ndichitireni chifundo. Mutume Lazaro kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi kuti aziziritse lilime langa,+ chifukwa ndikuzunzika m’moto wolilimawu.’+ 25 Koma Abulahamu anati, ‘Mwanawe, kumbukira kuti unalandiriratu zabwino zako zonse pamene unali moyo, ndipo Lazaro analandiriratu zinthu zoipa. Koma tsopano akusangalala kuno ndipo iwe ukuzunzika.+ 26 Komanso, paikidwa phompho lalikulu kwambiri+ pakati pa ife ndi anthu inu,+ moti ofuna kuolokera kumeneko kuchokera kuno sangathe. Komanso anthu sangaoloke kuchokera kumeneko kubwera kuno.’+ 27 Ndiyeno munthu wachuma uja anati, ‘Popeza zili choncho, ndikukupemphani atate kuti, mum’tumize kunyumba ya bambo anga. 28 Chifukwa ndili ndi abale anga asanu kumeneko, choncho apite akawapatse umboni wokwanira, kuti nawonso asabwere kumalo ozunzikira kuno.’ 29 Koma Abulahamu ananena kuti, ‘Kumeneko ali ndi Zolemba za Mose+ ndi Zolemba za aneneri,+ amvere zimenezo.’+ 30 Pamenepo iye anati, ‘Ayi chonde atate Abulahamu, pakuti ngati wina wochokera kwa akufa angapite kumeneko, iwo adzalapa ndithu.’ 31 Koma iye anamuuza kuti, ‘Ngati sakumvera Zolemba za Mose+ ndi Zolemba za aneneri, sangathekebe ngakhale wina atauka kwa akufa.’”
17 Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “N’zosatheka kuti pakhale popanda zopunthwitsa.+ Koma tsoka kwa munthu amene zopunthwitsazo zimadzera mwa iye!+ 2 Zingamuyendere bwino kwambiri atamukoloweka chimwala cha mphero m’khosi mwake ndi kumuponya m’nyanja,+ kusiyana n’kuti akhumudwitse mmodzi wa tiana iti.+ 3 Samalani ndithu. Ngati m’bale wako wachita tchimo um’dzudzule,+ ndipo akalapa umukhululukire.+ 4 Ngakhale akuchimwire maulendo 7 pa tsiku, n’kubwera kwa iwe maulendo 7, kudzanena kuti, ‘Ndalapa ine,’ umukhululukire ndithu.”+
5 Tsopano atumwiwo anauza Ambuye kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”+ 6 Pamenepo Ambuye anawayankha kuti: “Mukanakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mukanatha kuuza mtengo wa mabulosi uwu kuti, ‘Zuka pano, kadzibzale m’nyanjamo!’ ndipo ukanakumverani.+
7 “Ndani wa inu angauze kapolo wake amene wangofika kumene kuchokera ku ntchito yolima kapena yoweta nkhosa kuti, ‘Fika kutebulo kuno msanga udzadye’? 8 Kodi sadzamuuza kuti, ‘Ndikonzere chakudya chamadzulo, uvale epuloni ndi kunditumikira kufikira nditamaliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso udye ndi kumwa’? 9 Ndipo munthuyo sangamuyamike kapoloyo chifukwa zimene wachitazo ndi ntchito yake, si choncho kodi? 10 Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake.+ Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”
11 Tsopano pamene anali kupita ku Yerusalemu, anadutsa mkatikati mwa Samariya ndi Galileya.+ 12 Pamene anali kulowa m’mudzi wina, anakumana ndi amuna 10 akhate+ koma iwo anaima chapatali ndithu. 13 Kenako anafuula mokweza, kuti: “Yesu, Mlangizi,+ tichitireni chifundo!” 14 Yesu atawaona anawauza kuti: “Pitani mukadzionetse kwa ansembe.”+ Ndiyeno pamene anali kupita anayeretsedwa.+ 15 Mmodzi wa iwo ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, akutamanda Mulungu+ mokweza mawu. 16 Atafika anagwada pamaso pa Yesu n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ ndipo anamuthokoza. Munthu ameneyu anali Msamariya.+ 17 Pamenepo Yesu anati: “Amene ayeretsedwa si anthu 10 kodi? Nanga ena 9 ali kuti? 18 Kodi sanapezeke wina aliyense wobwerera kudzalemekeza Mulungu koma munthu wa mtundu wina yekhayu?” 19 Ndiyeno Yesu anauza munthuyo kuti: “Nyamuka uzipita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+
20 Tsopano Afarisi atamufunsa kuti ufumu wa Mulungu udzabwera liti,+ iye anawayankha kuti: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi ayi. 21 Ndipo anthu sadzanena kuti, ‘Onani kuno!’ kapena, ‘Uko!’+ Pakuti ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”+
22 Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Adzafika masiku pamene mudzalakalaka kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu koma simudzaliona.+ 23 Ndipo anthu adzakuuzani kuti, ‘Onani uko!’ kapena ‘Onani kuno!’+ Musadzapiteko kapena kuwatsatira.+ 24 Pakuti monga mphezi,+ mwa kung’anima kwake, imawala kuchokera mbali ina pansi pa thambo kukafika mbali ina pansi pa thambo, zidzakhalanso choncho ndi Mwana wa munthu.+ 25 Koma ayenera kukumana ndi mavuto ochuluka choyamba ndi kukanidwa ndi m’badwo uwu.+ 26 Komanso, monga zinachitikira m’masiku a Nowa,+ zidzachitikanso chimodzimodzi m’masiku a Mwana wa munthu.+ 27 M’masiku amenewo anthu anali kudya, kumwa, amuna anali kukwatira, akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa, ndipo chigumula chinafika ndi kuwononga anthu onsewo.+ 28 Chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika m’masiku a Loti.+ M’masiku amenewo anthu anali kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala ndi kumanga. 29 Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula n’kuwononga anthu onse.+ 30 Zidzakhalanso choncho pa tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekera.+
31 “Pa tsiku limenelo, munthu amene adzakhale padenga la nyumba koma katundu wake ali m’nyumbamo, asadzatsike kukatenga katundu wakeyo. Chimodzimodzinso munthu amene adzakhale ali m’munda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya m’mbuyo. 32 Kumbukirani mkazi wa Loti.+ 33 Aliyense wofunitsitsa kusunga moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake adzausunga.+ 34 Ndithu ndikukuuzani, Usiku umenewo amuna awiri adzagonera limodzi pamphasa. Mmodzi adzatengedwa, koma wina adzasiyidwa.+ 35 Amayi awiri adzakhala akupera limodzi pamphero. Mmodzi adzatengedwa, koma wina adzasiyidwa.”+ 36* —— 37 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti Ambuye?” Iye anawauza kuti: “Kumene kuli thupi lakufa,+ ziwombankhanga zidzasonkhana komweko.”+
18 Ndiyeno Yesu anawauza fanizo pofuna kuwasonyeza kufunika koti azipemphera nthawi zonse, osaleka.+ 2 Iye anati: “Mumzinda winawake munali woweruza wina amene anali wosaopa Mulungu ndiponso wosasamala za munthu. 3 Koma mumzindawo munali mkazi wina wamasiye ndipo anali kupitapita+ kwa woweruza uja kukamupempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene akutsutsana nane, kuti pachitike chilungamo.’ 4 Kwa kanthawi ndithu woweruzayo sankafuna, koma pambuyo pake ananena mumtima mwake kuti, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu, 5 ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa mkazi wamasiyeyu. Ndichita zimenezi kuti asapitirize kumangobwera ndi kundisautsa kwambiri,+ chifukwa mkazi ameneyu akundivutitsa+ mosalekeza.’” 6 Kenako Ambuye anati: “Mwamvatu zimene woweruzayo ananena ngakhale kuti anali wosalungama! 7 Ndithu, ngakhale kuti Mulungu amalezera mtima+ osankhidwa ake, kodi sadzaonetsetsa kuti chilungamo+ chachitika kwa iwo, amene amafuulira kwa iye usana ndi usiku? 8 Ndithu ndikukuuzani, Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga.+ Koma, Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro padziko lapansi?”
9 Yesu ananenanso fanizo lotsatirali kwa ena odzidalira, odziona ngati olungama+ amenenso amaona ena onse ngati opanda pake.+ Iye anati: 10 “Anthu awiri anapita m’kachisi kukapemphera. Mmodzi anali Mfarisi, winayo anali wokhometsa msonkho. 11 Mfarisi uja anaimirira+ ndi kuyamba kupemphera+ mumtima mwake. Iye anati, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu.+ 12 Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu ndipo ndimapereka chakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’+ 13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+ 14 Ndithu ndikukuuzani, Munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kukhala wolungama kwambiri+ kusiyana ndi wina uja, chifukwa aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.”+
15 Pamenepo anthu anayamba kumubweretsera ana kuti awakhudze ndi manja ake, koma ophunzirawo ataona zimenezo anayamba kuwakalipira.+ 16 Komabe Yesu anaitana anawo. Iye anati: “Alekeni anawo abwere kwa ine, musawaletse ayi. Pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.+ 17 Ndithu ndikukuuzani, Aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa n’komwe mu ufumuwo.”+
18 Tsopano wolamulira wina anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 19 Yesu anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+ 20 Iwe umadziwa malamulo+ akuti, ‘Usachite chigololo,+ Usaphe munthu,*+ Usabe,+ Usapereke umboni wonama+ ndiponso lakuti, Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’”+ 21 Pamenepo iye anati: “Zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamng’ono.”+ 22 Atamva zimenezo, Yesu anamuuza kuti: “Pali chinthu chimodzi chimene chikusowekabe mwa iwe: Kagulitse zinthu zonse zimene uli nazo n’kugawa ndalamazo kwa anthu osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 23 Iye atamva zimenezi, anamva chisoni kwambiri, chifukwa anali wolemera kwabasi.+
24 Yesu anamuyang’ana n’kunena kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu a ndalama adzalowe mu ufumu wa Mulungu!+ 25 Kunena zoona, n’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”+ 26 Amene anamva zimenezi anati: “Ndiye angapulumuke ndani?” 27 Iye anawauza kuti: “Zinthu zosatheka ndi anthu n’zotheka ndi Mulungu.”+ 28 Koma Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu ndi kukutsatirani.”+ 29 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Palibe amene wasiya nyumba, mkazi, abale, makolo kapena ana, chifukwa cha ufumu wa Mulungu+ 30 amene sadzapeza zochuluka kwambiri kuposa zimenezi m’nthawi ino, ndipo m’nthawi* ikubwerayo moyo wosatha.”+
31 Kenako anatengera pambali ophunzira 12 aja ndi kuwauza kuti: “Tamverani! Tsopano tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zinalembedwa ndi aneneri,+ zokhudza Mwana wa munthu zikakwaniritsidwa.+ 32 Mwachitsanzo, akamupereka kwa anthu a mitundu ina ndipo akamuseka,+ kum’chitira chipongwe+ ndi kumulavulira.+ 33 Akakamaliza kumukwapula+ akamupha,+ koma tsiku lachitatu iye adzauka.”+ 34 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la chilichonse cha zimenezi. Mawu amenewa anabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe zimene zinanenedwazo.+
35 Tsopano pamene anali kuyandikira ku Yeriko, munthu wina wakhungu anakhala pansi m’mphepete mwa msewu n’kumapemphapempha.+ 36 Atamva khamu la anthu likudutsa chapomwepo, anafunsa chimene chinali kuchitika. 37 Iwo anamuuza kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!”+ 38 Atamva zimenezo anafuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!”+ 39 Ndiyeno amene anali patsogolo anayamba kumudzudzula mwamphamvu kuti akhale chete. Koma m’pamenenso iye anafuula kwambiri kuti: “Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo.”+ 40 Choncho Yesu anaima ndi kulamula kuti munthuyo apite naye kwa iye.+ Atafika pafupi, Yesu anamufunsa kuti: 41 “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”+ Iye anayankha kuti: “Ambuye, ndithandizeni kuti ndiyambe kuona.”+ 42 Choncho Yesu anamuuza kuti: “Yamba kuona, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ 43 Nthawi yomweyo anayamba kuona,+ ndipo anayamba kumutsatira akulemekeza Mulungu.+ Komanso anthu onse, ataona zimenezi, anatamanda Mulungu.
19 Ndiyeno Yesu analowa mu Yeriko,+ koma anali kungodutsamo. 2 Kumeneko kunali munthu wina dzina lake Zakeyu. Iyeyu anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera. 3 Zakeyu anali kufunitsitsa kuona+ Yesu kuti ndi wotani, koma sanathe kutero chifukwa cha khamu la anthu, pakuti anali wamfupi. 4 Choncho anathamangira kutsogolo n’kukwera mumtengo wamkuyu kuti athe kumuona, chifukwa anali kudzera njira imeneyo. 5 Yesu atafika pamalopo, anayang’ana m’mwambamo n’kumuuza kuti: “Zakeyu, fulumira tsika, chifukwa lero ndiyenera kukakhala m’nyumba mwako.” 6 Atamva zimenezo anatsika mofulumira, ndipo mosangalala anamulandira m’nyumba mwake monga mlendo wake. 7 Koma anthu ataona Yesu akulowa m’nyumbamo, onse anayamba kung’ung’udza,+ kuti: “Akupita kukakhala ndi munthu wochimwa.” 8 Koma Zakeyu anaimirira ndi kuuza Ambuye kuti: “Ambuye, ine ndipereka ndithu hafu ya chuma changa kwa osauka. Ndipo chilichonse chimene ndinalanda munthu aliyense pomunamizira mlandu+ ndibweza kuwirikiza kanayi.”+ 9 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Lero chipulumutso chafika panyumba ino, chifukwa nayenso ndi mwana wa Abulahamu.+ 10 Pakuti Mwana wa munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa anthu osochera.”+
11 Pamene iwo anali kumvetsera zimenezi, iye anawonjezapo fanizo, chifukwa anali pafupi ndi Yerusalemu ndipo anthu anali kuganiza kuti ufumu wa Mulungu uonekera nthawi yomweyo.+ 12 Choncho iye ananena kuti: “Munthu wina wa m’banja lachifumu anapita kudziko lakutali kuti akalandire ufumu ndi kubwerako.+ 13 Ndiyeno anaitana akapolo ake 10 ndi kuwapatsa ndalama 10 za mina n’kuwauza kuti, ‘Muchite malonda mpaka nditabwera.’+ 14 Koma nzika zinzake zinadana naye+ ndipo m’mbuyo muno zinatumiza akazembe kuti apite akanene kuti, ‘Ife sitikufuna kuti munthu uyu akhale mfumu yathu.’+
15 “Atabwerera kwawo pambuyo polandira ufumuwo, analamula kuti akapolo ake aja amene anawapatsa ndalama zasiliva abwere kwa iye, kuti awerengerane ndi kuona mmene apindulira pa malonda awo.+ 16 Woyamba anafika ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija inapindula ndalama zina 10 za mina.’+ 17 Iye anamuuza kuti, ‘Unagwira ntchito, ndiwe kapolo wabwino! Chifukwa wasonyeza kukhulupirika pa chinthu chaching’ono, ndakupatsa ulamuliro woyang’anira mizinda 10.’+ 18 Kenako wachiwiri anafika, ndipo anati, ‘Ambuye ndalama yanu ija ya mina yapindula zinanso zisanu.’+ 19 Iye anauzanso ameneyu kuti, ‘Nawenso ukhala woyang’anira mizinda isanu.’+ 20 Tsopano panafika wina ndipo ananena kuti, ‘Ambuye, ndalama yanu ya mina ija nayi. Ndinaimanga pansalu ndi kuisunga. 21 Ndinachita zimenezi chifukwa ndinali kukuopani. Inutu ndinu munthu wouma mtima. Mumatenga zimene simunasungitse ndi kukolola zimene simunafese.’+ 22 Iye anamuuza kuti, ‘Ndikuweruza mwa zotuluka pakamwa pako,+ kapolo woipa iwe. Ukuti unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wotenga zimene sindinasungitse ndi kukolola zimene sindinafese?+ 23 Nangano n’chifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga yasilivayo kwa osunga ndalama? Ukanatero, ine pobwera ndikanaitenga limodzi ndi chiwongoladzanja chake.’+
24 “Atatero anauza anthu amene anaima chapafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya mina imeneyo ndi kuipereka kwa winayo amene ali ndi ndalama 10.’+ 25 Koma iwo anamuuza kuti, ‘Ambuye, iyetu ali nazo ndalama za mina 10!’ . . . 26 ‘Ndithu ndikukuuzani, Aliyense amene ali nazo, adzamuwonjezera zochuluka, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 27 Komanso adani angawa, amene sanafune kuti ine ndikhale mfumu yawo, bwerani nawo kuno muwaphe ine ndikuona.’”+
28 Choncho atatsiriza kunena zimenezi, anapitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu.+ 29 Tsopano atayandikira ku Betefage ndi Betaniya paphiri lotchedwa phiri la Maolivi,+ anatumiza ophunzira ake awiri.+ 30 Iye anawauza kuti: “Pitani m’mudzi umene mukuuonawo, ndipo mukalowa mmenemo mukapeza bulu wamng’ono wamphongo atamumangirira, amene munthu sanakwerepo chiyambire. Mukamumasule n’kubwera naye kuno.+ 31 Koma aliyense akakakufunsani kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukumasula buluyu?’ Mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna.’”+ 32 Choncho otumidwawo ananyamuka ndipo anakam’pezadi mmene iye anawauzira.+ 33 Koma mmene anali kumasula buluyo, eniake anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukumasula buluyu?”+ 34 Iwo anayankha kuti: “Ambuye akumufuna.”+ 35 Pamenepo iwo anamutenga ndi kupita naye kwa Yesu. Kenako iwo anaponya malaya awo akunja pabuluyo ndi kukwezapo Yesu.+
36 Pamene anali kuyenda,+ anthu anali kuyala malaya awo akunja mumsewu.+ 37 Atangofika pafupi ndi msewu wochokera m’phiri la Maolivi khamu lonse la ophunzirawo linayamba kukondwera ndi kutamanda Mulungu mokweza mawu chifukwa cha ntchito zamphamvu zimene anaona.+ 38 Iwo anali kunena kuti: “Wodalitsidwa Iye wobwera monga Mfumu m’dzina la Yehova!+ Mtendere kumwamba, ndi ulemerero kumwambamwambako!”+ 39 Koma Afarisi ena m’khamulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anuwa.”+ 40 Poyankha iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, ngati awa atakhala chete, miyala+ ingathe kufuula.”
41 Tsopano atayandikira mzinda wa Yerusalemu, anaona mzindawo n’kuyamba kuulirira.+ 42 Iye anati: “Iwe ukanazindikira+ lero zinthu zamtendere . . . koma tsopano zabisika kuti usathe kuziona.+ 43 Chifukwa masiku adzakufikira pamene adani ako adzamanga mpanda+ wazisonga+ kukuzungulira.+ Adaniwo adzakutsekereza ndi kukusautsa+ kuchokera kumbali zonse. 44 Iwo adzakuwononga+ limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake+ mwa iwe, chifukwa sunazindikire kuti nthawi yokuyendera inali itakwana.”+
45 Ndiyeno analowa m’kachisi n’kuyamba kuthamangitsa anthu amene anali kugulitsamo zinthu,+ 46 ndi kuwauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzakhala nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+
47 Ndipo anali kuphunzitsa m’kachisimo tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, alembi ndi akuluakulu a anthu anafunitsitsa kumupha.+ 48 Komabe anasowa chochita chifukwa anthu ambiri anali kungomuunjirira kuti amumvetsere ndipo sanali kusiyana naye.+
20 Tsiku lina pamene anali kuphunzitsa anthu m’kachisi ndi kulengeza uthenga wabwino, panafika ansembe aakulu, alembi pamodzi ndi akulu.+ 2 Iwo anamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 3 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi, ndipo mundiyankhe:+ 4 Kodi ubatizo wa Yohane unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu?”+ 5 Pamenepo iwo anayamba kukambirana okhaokha kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye anena kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+ 6 Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala,+ chifukwa iwo akukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane+ anali mneneri.”+ 7 Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera. 8 Pamenepo Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”+
9 Ndiyeno iye anayamba kuuza anthuwo fanizo ili: “Munthu wina analima munda wa mpesa,+ ndipo anasiya mundawo m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali ndithu.+ 10 Koma nyengo ya zipatso itakwana anatumiza kapolo+ wake kwa alimiwo,+ kuti akamupatseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo.+ Komano alimiwo anamumenya ndi kumubweza chimanjamanja.+ 11 Koma iye anawatumiziranso kapolo wina. Ameneyonso anamumenya ndi kumuchitira chipongwe, ndipo anamubweza chimanjamanja.+ 12 Anatumizanso wachitatu.+ Uyunso anamuvulaza ndi kumuponya kunja. 13 Zitatero mwini munda wa mpesa uja anati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Chabwino, nditumiza mwana wanga wokondedwa.+ Mwana wanga yekhayu ayenera kuti akamulemekeza ndithu.’ 14 Alimiwo atamuona anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa. Tiyeni timuphe kuti cholowacho chikhale chathu.’+ 15 Atatero anamutulutsa+ m’munda wa mpesawo ndi kumupha.+ Pamenepa, kodi mwini munda wa mpesa uja adzachita chiyani kwa alimiwo?+ 16 Adzabwera ndi kupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.”+
Atamva zimenezi iwo anati: “Ayi zisatero ndithu!” 17 Koma iye anawayang’ana ndi kunena kuti: “Pajatu malemba amati, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana,+ umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? 18 Aliyense wogwera pamwala umenewo adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere,+ udzam’pereratu.”+
19 Tsopano alembi ndi ansembe aakulu aja, pozindikira kuti iye anali kunena za iwo mufanizolo, anayesetsa kupeza mpata kuti amugwire ola lomwelo, koma anaopa anthu.+ 20 Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, n’cholinga choti akamukole+ m’mawu ake, kuti akamupereke ku boma ndi kwa bwanamkubwa.+ 21 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti mumanena ndi kuphunzitsa molondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi.+ 22 Kodi n’kololeka kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”+ 23 Koma Yesu anazindikira ndale zawo ndipo anawauza kuti:+ 24 “Ndionetseni khobidi la dinari. Kodi nkhope ndi mawu ali pamenepo n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”+ 25 Iye anawauza kuti: “Chotero perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ 26 Pamenepo iwo analephera kumutapa m’kamwa pa zimene ananenazi pamaso pa anthu, mwakuti pothedwa nzeru ndi yankho lake, anangokhala chete kusowa chonena.+
27 Koma Asaduki ena, amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa anafika+ ndi kuyamba kumufunsa, 28 kuti: “Mphunzitsi, Mose+ anatilembera kuti, ‘Ngati munthu wamwalira n’kusiya mkazi amene sanabereke naye ana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.’+ 29 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anatenga mkazi, koma anamwalira wopanda mwana.+ 30 Wachiwirinso chimodzimodzi. 31 Kenako wachitatu anamutenga. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja: onse anamwalira osasiya ana.+ 32 Pa mapeto pake mkazi uja nayenso anamwalira.+ 33 Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”+
34 Yesu anawayankha kuti: “Ana a m’nthawi* ino amakwatira+ ndi kukwatiwa. 35 Koma amene ayesedwa oyenerera+ kudzapeza moyo pa nthawi* imeneyo+ ndi kudzaukitsidwa kwa akufa+ sadzakwatira kapena kukwatiwa. 36 Ndiponso iwo sadzafanso,+ chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu mwa kukhala ana a kuuka kwa akufa.+ 37 Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza m’nkhani ya chitsamba cha minga.+ M’nkhani imeneyo iye ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+ 38 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.”+ 39 Poyankha ena mwa alembiwo anati: “Mphunzitsi, mwanena bwino.” 40 Ananena zimenezi chifukwa sanathenso kulimba mtima kuti amufunse funso lina ngakhale limodzi.
41 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 42 Pakuti Davide mwiniyo ananena m’buku la Masalimo kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43 kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”’+ 44 Chotero Davide anamutcha ‘Ambuye.’ Nanga akukhala bwanji mwana wake?”
45 Kenako, anthu onse akumvetsera, iye anauza ophunzirawo kuti:+ 46 “Chenjerani ndi alembi. Iwo amakonda kuyendayenda atavala mikanjo. Amakonda kupatsidwa moni m’misika ndi kukhala m’mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.+ 47 Iwo ndi amene amadyerera nyumba za akazi amasiye,+ ndipo mwachiphamaso amapereka mapemphero ataliatali. Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.”+
21 Tsopano atakweza maso anaona anthu olemera akuponya zopereka zawo moponyamo zopereka.+ 2 Kenako anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobidi tiwiri tating’ono mmenemo.+ 3 Ndipo iye anati: “Kunena zoona, Mkazi wamasiyeyu, ngakhale kuti ndi wosauka, waponya zochuluka kuposa onse amene aponya.+ 4 Pakuti onsewa aponya zopereka zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake.”+
5 Nthawi ina, anthu ena anali kulankhula za kachisi, mmene anam’kongoletsera ndi miyala yochititsa kaso komanso mphatso zoperekedwa kwa Mulungu.+ 6 Choncho iye anati: “Kunena za zinthu izi mukuzionazi, masiku adzafika pamene sipadzakhala mwala wosiyidwa pano pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+ 7 Pamenepo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti kwenikweni, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zili pafupi kuchitika n’chiyani?”+ 8 Iye anayankha kuti: “Samalani kuti asadzakusocheretseni.+ Pakuti ambiri adzabwera m’dzina langa, n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ adzanenanso kuti, ‘Nthawi ija yayandikira.’+ Musadzawatsatire. 9 Komanso, mukadzamva phokoso la nkhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha.+ Pakuti zimenezi ziyenera kuchitika choyamba, koma mapeto sadzafika nthawi yomweyo.”
10 Anapitiriza kuwauza kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina,+ ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ 11 Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala+ m’malo osiyanasiyana. Kudzaoneka zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.+
12 “Koma zonsezi zisanachitike, anthu adzakugwirani ndi kukuzunzani,+ adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakutengerani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa.+ 13 Umenewu udzakhala mpata wanu wochitira umboni.+ 14 Chotero tsimikizirani m’mitima yanu kuti musachite kukonzekera zoti mukayankhe podziteteza,+ 15 chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+ 16 Komanso makolo anu enieniwo,+ abale anu, anthu oyandikana nanu ndi mabwenzi anu, adzakuperekani, ndipo adzapha ena a inu.+ 17 Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ 18 Komatu ngakhale tsitsi limodzi lokha+ la m’mutu mwanu silidzawonongeka ayi. 19 Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.+
20 “Chinanso, mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu,+ mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira.+ 21 Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madera akumidzi asadzalowe mumzindawo,+ 22 chifukwa amenewa ndi masiku obwezera chilango, kuti zonse zimene zinalembedwa zikwaniritsidwe.+ 23 Tsoka kwa akazi apakati ndi kwa oyamwitsa ana m’masiku amenewo!+ Pakuti m’dzikoli mudzakhala mavuto aakulu ndi mkwiyo pa anthu awa. 24 Anthu adzaphedwa ndi lupanga ndiponso kutengedwa ukapolo kupita nawo ku mitundu ina yonse.+ Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikira nthawi zoikidwiratu+ za anthu a mitundu inawo zitakwanira.
25 “Komanso, padzakhala zizindikiro padzuwa,+ mwezi ndi nyenyezi. Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika, ndipo adzathedwa nzeru chifukwa cha mkokomo wa nyanja+ ndi kuwinduka kwake.+ 26 Mwakuti anthu adzakomoka chifukwa cha mantha+ ndi kuyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi+ kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.+ 27 Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera mumtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.+ 28 Koma zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.”
29 Atanena izi, anawauza fanizo kuti: “Onetsetsani mtengo wa mkuyu ndi mitengo ina yonse:+ 30 Mukaona mitengo ikuphukira, mumadziwa ndithu kuti tsopano dzinja lili pafupi.+ 31 Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.+ 32 Ndithu ndikukuuzani, M’badwo umenewu sudzatha wonse kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.+ 33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka,+ koma mawu anga sadzachoka ayi.+
34 “Koma samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri,+ ndi nkhawa+ za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa+ 35 ngati msampha.+ Pakuti lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi.+ 36 Chotero khalani maso+ ndipo muzipemphera mopembedzera+ nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.”+
37 Masana Yesu anali kuphunzitsa m’kachisi,+ koma usiku anali kupita kukagona kuphiri lotchedwa phiri la Maolivi.+ 38 Ndipo anthu onse+ anali kulawirira m’mawa kwambiri kupita kwa iye kukachisi kuti akamumvetsere.
22 Tsopano chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa, chotchedwanso kuti Pasika,+ chinali kuyandikira. 2 Komanso ansembe aakulu ndi alembi anali kufunafuna njira yabwino yophera Yesu,+ pakuti anali kuopa anthu.+ 3 Koma Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja.+ 4 Iye anapita kukakambirana ndi ansembe aakulu ndi oyang’anira kachisi za njira yabwino yomuperekera kwa iwo.+ 5 Iwo anakondwa, ndipo anagwirizana kuti amupatse ndalama zasiliva.+ 6 Choncho iye anavomereza, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke kwa iwo popanda khamu la anthu pafupi.+
7 Tsopano tsiku la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa linafika, tsiku loyenera kupha nyama yoperekera nsembe ya pasika.+ 8 Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane kuti: “Pitani mukatikonzere+ pasika kuti tidye.” 9 Iwo anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti?” 10 Iye anawayankha kuti:+ “Mukalowa mumzinda, mwamuna wina wosenza mtsuko wa madzi akumana nanu. Mukamutsatire kunyumba imene akalowe.+ 11 Ndipo mukauze mwininyumba imeneyo kuti, ‘Mphunzitsi akufunsa kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti, mmene ine ndidyeremo pasika pamodzi ndi ophunzira anga?”’+ 12 Ndiyeno munthu ameneyo akakusonyezani chipinda chachikulu cham’mwamba chokonzedwa bwino. Mukakonzere mmenemo.”+ 13 Choncho ananyamuka ndi kupita. Kumeneko zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo anakonza pasika kumeneko.+
14 Nthawi itakwana, anakhala patebulo la chakudya, atumwi akenso anali naye limodzi.+ 15 Ndiyeno anawauza kuti: “Ndinali wofunitsitsa kudya pasika uyu limodzi ndi inu ndisanalowe m’masautso. 16 Pakuti ndikukuuzani, sindidzadyanso pasika kufikira zonse zimene pasikayu akuimira zitakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”+ 17 Ndiyeno analandira kapu+ ndi kuyamika, kenako anati: “Landirani kapu iyi, nonse imwani mopatsirana. 18 Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utafika.”+
19 Kenako anatenga mkate.+ Atayamika anaunyemanyema n’kuwapatsa, ndipo anati: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu.+ Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+ 20 Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu+ atadya chakudya chamadzulocho. Iye anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano+ pamaziko a magazi anga,+ amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.+
21 “Koma taonani! Wondipereka+ ndili naye limodzi patebulo pompano.+ 22 Chifukwa Mwana wa munthu akuchoka malinga n’zimene zinanenedweratu.+ Koma, tsoka kwa munthu amene akumupereka!”+ 23 Choncho anayamba kufunsana ndi kukambirana pakati pawo za amene anakonza chiwembu chimenecho.+
24 Komanso, panabuka mkangano woopsa pakati pawo za amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.+ 25 Koma Yesu anawauza kuti: “Mafumu a mitundu ya anthu amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amatchedwa Opereka zabwino.+ 26 Inu musakhale otero.+ Koma amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamng’ono kwambiri pa nonsenu,+ ndipo amene ali mtsogoleri akhale wotumikira.+ 27 Kodi wamkulu ndani, amene akudya patebulo kapena amene akutumikira? Si amene akudya patebulo kodi? Koma ine ndili pakati panu monga wotumikira.+
28 “Komabe, inu mwakhalabe ndi ine+ m’mayesero anga.+ 29 Choncho ndikuchita nanu pangano,+ mmene Atate wanga wachitira pangano la ufumu ndi ine,+ 30 kuti mukadye+ ndi kumwa patebulo langa mu ufumu wanga,+ ndipo mukakhala m’mipando yachifumu+ kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.
31 “Simoni, Simoni! Ndithu Satana+ akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu.+ 32 Koma ine ndakupempherera+ iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse+ abale ako.” 33 Pamenepo iye anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu limodzi kundende kapena kufa nanu limodzi.”+ 34 Koma iye anati: “Ndikukuuza iwe Petulo, Tambala asanalire lero, undikana katatu kuti sundidziwa.”+
35 Yesu anauzanso ophunzirawo kuti: “Pamene ndinakutumizani+ opanda chikwama cha ndalama, thumba la chakudya, kapena nsapato, munasowa kanthu kodi?” Iwo anati: “Ayi!” 36 Pamenepo anawauza kuti: “Koma tsopano amene ali ndi chikwama cha ndalama achitenge, chimodzimodzinso thumba la chakudya. Ndipo amene alibe lupanga agulitse malaya ake akunja n’kugula lupanga. 37 Pakuti ndikukuuzani kuti mawu olembedwawa ayenera kukwaniritsidwa mwa ine. Mawuwo ndi akuti, ‘Ndipo anamutenga ngati mmodzi wa anthu osamvera malamulo.’+ Pakuti chimene chikukhudza ine chikukwaniritsidwa.”+ 38 Pamenepo iwo anati: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awiri awa.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanira.”
39 Atachoka kumeneko anapita kuphiri la Maolivi monga anali kuchitira nthawi zonse. Ophunzira nawonso anamutsatira.+ 40 Atafika pamalowo anauza ophunzirawo kuti: “Pempherani kosalekeza, kuti musalowe m’mayesero.”+ 41 Iye analekana nawo ndi kuyenda kamtunda, kutalika kwake ngati pamene pangagwere mwala munthu atauponya. Kumeneko anagwada ndi kuyamba kupemphera, 42 kuti: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu chifuniro chanu chichitike,+ osati changa.”+ 43 Pamenepo mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye ndi kumulimbikitsa.+ 44 Koma atazunzika koopsa mumtima mwake, anapitiriza kupemphera ndi mtima wonse+ ndipo thukuta lake linaoneka ngati madontho amagazi amene akugwera pansi.+ 45 Kenako ananyamuka pamene anali kupemphererapo n’kupita kwa ophunzira aja. Koma anawapeza atagona chifukwa cha chisoni.+ 46 Iye anawauza kuti: “Mukugona chifukwa chiyani? Dzukani, pitirizani kupemphera kuti musalowe m’mayesero.”+
47 Mawu adakali m’kamwa, panafika khamu la anthu, limodzi ndi Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, akuwatsogolera.+ Ndiyeno Yudasi anapita pamene panali Yesu kukamupsompsona.+ 48 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa munthu mwa kupsompsona?”+ 49 Anthu amene anali naye pafupi ataona zimene zinali kuchitika, anati: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?”+ 50 Wina wa iwo anatemadi kapolo wa mkulu wa ansembe ndi kuduliratu khutu lake lakumanja.+ 51 Koma Yesu anati: “Basi! Lekani zimenezi.” Ndipo anagwira khutu lija ndi kumuchiritsa.+ 52 Yesu pamenepo anafunsa ansembe aakulu, oyang’anira kachisi ndi akulu amene anam’londola kumeneko, kuti: “Bwanji mwabwera ndi malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba?+ 53 Tsiku ndi tsiku ndinali nanu m’kachisi+ koma simunandigwire.+ Koma ino tsopano ndi nthawi yanu+ komanso nthawi ya ulamuliro+ wa mdima.”+
54 Pamenepo anamugwira ndi kumutenga,+ ndipo anakamulowetsa m’nyumba ya mkulu wa ansembe.+ Koma Petulo anali kuwatsatira chapatali.+ 55 Atasonkha moto mkati mwa bwalo ndi kukhala pansi onse pamodzi, Petulo nayenso anakhala nawo pamenepo.+ 56 Koma mayi wina wantchito anamuona atakhala pafupi ndi moto wowala ndipo anamuyang’ana ndi kunena kuti: “Bambo awanso anali naye limodzi.”+ 57 Koma iye anakana+ kuti: “Mayi iwe, ameneyu ine sindimudziwa ayi.”+ 58 Patapita kanthawi pang’ono, munthu wina anamuona ndi kunena kuti: “Iwenso uli m’gulu la ophunzira ake.” Koma Petulo anati: “Munthu iwe, si ine ayi.”+ 59 Patapita pafupifupi ola lathunthu, munthu winanso anayamba kunena motsimikiza kuti: “Ndithu sindikukayika, munthu uyunso anali naye limodzi, ndipo iyeyu ndi Mgalileya!”+ 60 Koma Petulo anati: “Munthu iwe, ine sindikudziwa zimene ukunena.” Nthawi yomweyo, mawu ali m’kamwa, tambala analira.+ 61 Pamenepo Ambuye anacheuka ndi kuyang’ana Petulo, ndipo Petulo anakumbukira mawu amene Ambuye anamuuza aja, akuti: “Tambala asanalire lero, undikana katatu.”+ 62 Ndipo anatuluka panja ndi kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.+
63 Tsopano amuna amene anagwira Yesu aja anayamba kumuchitira zachipongwe,+ ndi kumumenya.+ 64 Anali kumuphimba kumaso ndi kumufunsa kuti: “Losera. Wakumenya ndani?”+ 65 Ndipo anapitiriza kunena zambiri zomunyoza.+
66 Kenako kutacha, bungwe la akulu, kuphatikizapo ansembe aakulu komanso alembi, anasonkhana pamodzi,+ ndipo anamutengera kuholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda.* Kumeneko iwo anati:+ 67 “Tiuze ngati ndiwe Khristu.”+ Koma iye anawayankha kuti: “Ngakhale ndikuuzeni, simukhulupirira.+ 68 Komanso nditakufunsani, simungathe n’komwe kuyankha.+ 69 Koma kuyambira tsopano Mwana wa munthu+ adzakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu la Mulungu.”+ 70 Atanena izi onse anati: “Kodi ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anawayankha kuti: “Inunso mukunena nokha+ kuti ndine amene.” 71 Iwo anati: “Tifuniranjinso umboni wina?+ Apatu tadzimvera tokha kuchokera pakamwa pake.”+
23 Pamenepo khamu lonselo linanyamuka, onse pamodzi, n’kupita naye kwa Pilato.+ 2 Ndiyeno anayamba kumuneneza+ kuti: “Ife tapeza munthu uyu akupandutsa+ mtundu wathu ndi kuletsa anthu kuti asamakhome msonkho+ kwa Kaisara, komanso iyeyu akunena kuti ndi Khristu mfumu.”+ 3 Tsopano Pilato anamufunsa funso kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” Pomuyankha iye anati: “Mukunena nokha.”+ 4 Pamenepo Pilato anauza ansembe aakulu ndi khamu la anthulo kuti: “Sindikupeza mlandu uliwonse mwa munthu uyu.”+ 5 Koma iwo anaumirira kuti: “Iyeyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, ngakhalenso kuyambira ku Galileya mpaka kudzafika kuno.” 6 Atamva zimenezo, Pilato anafunsa ngati munthuyu ndi Mgalileya. 7 Ndiyeno, atadziwa kuti ndi wochokera m’chigawo cholamulidwa ndi Herode,*+ anamutumiza kwa Herode, amene m’masiku amenewo anali mu Yerusalemu.
8 Herode ataona Yesu anakondwera kwambiri, chifukwa kwa nthawi yaitali ndithu anali kufunitsitsa kuti amuone+ popeza anali kumva+ za iye. Komanso anali kuyembekezera kuona chizindikiro chimene iye angachite. 9 Tsopano anayamba kumufunsa zambiri, koma iye sanayankhe.+ 10 Komabe ansembe aakulu ndi alembi anali kumangonyamukanyamuka ndi kumuneneza mwaukali.+ 11 Pamenepo Herode pamodzi ndi asilikali ake omulondera anamupeputsa.+ Anamuchitira zachipongwe+ mwa kumuveka chovala chonyezimira ndipo anamutumizanso kwa Pilato. 12 Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato+ anakhala mabwenzi tsopano, koma m’mbuyo monsemo izi zisanachitike, anali pa udani.
13 Ndiyeno Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulira ndi anthu ena 14 ndi kuwauza kuti: “Inu mwabweretsa munthu uyu kwa ine monga wolimbikitsa anthu kuukira. Koma mwaona nokha pano! Inetu ndamufunsa pamaso panu, ndipo sindinamupeze ndi chifukwa+ chomuimbira milandu imene mukumunenezayi. 15 Ndipotu ngakhale Herode sanam’peze ndi mlandu, n’chifukwa chake wam’bweza kwa ife. Ndithudi ameneyu sanachite chilichonse choyenera chilango cha imfa.+ 16 Choncho ndingomukwapula+ ndi kumumasula.” 17* —— 18 Koma khamu lonse linafuulira pamodzi kuti: “Ameneyu muthane naye basi,+ koma ife mutimasulire Baraba!”+ 19 (Munthu ameneyu anaponyedwa m’ndende chifukwa cha kuukira boma kumene kunachitika mumzindawo, komanso chifukwa chopha munthu.) 20 Pilato analankhula nawo kachiwiri, chifukwa anali wofunitsitsa kumasula Yesu.+ 21 Pamenepo anthuwo anayamba kufuula kuti: “M’pachikeni! M’pachikeni!”+ 22 Anawafunsa kachitatu kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani? Ine sindikumupeza ndi chifukwa chilichonse chomuphera, choncho ndimukwapula ndi kumumasula.”+ 23 Atamva izi, anayamba kumuumiriza mokweza mawu, ndi kumupempha kuti Yesu apachikidwe basi. Anthuwo anali kufuula mwamphamvu moti Pilato anangololera.+ 24 Choncho Pilato anapereka chiweruzo chokwaniritsa zofuna za anthuwo.+ 25 Iye anamasula+ munthu woponyedwa m’ndende pa mlandu woukira boma ndi kupha munthu, amenenso anthuwo anapempha kuti amumasule. Koma Yesu anamupereka m’manja mwawo kuti zofuna zawo zichitike.+
26 Pamene anali kupita naye, iwo anagwira Simoni, nzika ya ku Kurene, amene anali kuchokera kudera lakumidzi. Iwo anamusenzetsa mtengo wozunzikirapo,* kuti aunyamule ndi kumatsatira pambuyo pa Yesu.+ 27 Koma khamu lalikulu la anthu linali kumutsatira pamodzi ndi amayi ambiri amene anali kudziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni ndipo anali kumulirira. 28 Yesu anacheukira amayiwo ndi kunena kuti: “Ana aakazi a Yerusalemu inu, lekani kundilirira. Koma mudzilirire nokha ndi ana anu.+ 29 Chifukwa masiku akubwera pamene anthu adzanena kuti, ‘Odala ndi akazi osabereka, amene sanaberekepo, komanso amene mabere awo sanayamwitsepo!’+ 30 M’masiku amenewo iwo adzayamba kuuza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’+ 31 Pakuti ngati akuchita izi pamene mtengo uli wauwisi, kuli bwanji mtengowo ukadzauma?”+
32 Anthuwo anatenganso amuna ena awiri ochita zoipa, kuti akawaphe limodzi ndi Yesu.+ 33 Tsopano atafika pamalo otchedwa Chibade,+ anamupachika pamenepo pamodzi ndi amuna ochita zoipawo. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja, wina kumanzere kwake.+ 34 [[Koma Yesu anati: “Atate, akhululukireni,+ chifukwa sakudziwa chimene akuchita.”]]* Ndipo iwo anagawana malaya ake mwa kuchita maere.+ 35 Anthu anangoima chilili kuonerera zochitikazo.+ Koma olamulira anali kumunyogodola kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, m’lekeni adzipulumutse yekha,+ ngati iyeyu alidi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwa.”+ 36 Asilikali nawonso anamuchitira zachipongwe,+ anamuyandikira ndi kumupatsa vinyo wowawasa+ 37 ndi kunena kuti: “Ngati ulidi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” 38 Pamwamba pake analembapo mawu akuti: “Uyu ndiye mfumu ya Ayuda.”+
39 Komanso mmodzi wa ochita zoipa amene anapachikidwa naye pamodziwo anayamba kumulankhulira zachipongwe+ kuti: “Kodi si iwe Khristu? Dzipulumutse wekha, limodzi ndi ife.” 40 Poyankha mnzake uja anamudzudzula kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu eti, poona kuti nawenso ukulandira chilango chofanana ndi cha munthu ameneyu?+ 41 Ifetu m’pake kulangidwa chonchi, pakuti tikulandiriratu zonse zotiyenera malinga ndi zimene tinachita. Koma munthu uyu sanalakwe chilichonse.”+ 42 Kenako anapitiriza kunena kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.”+ 43 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine+ m’Paradaiso.”+
44 Tsopano nthawi inali cha m’ma 12 koloko masana,* koma kunagwa mdima padziko lonse lapansi mpaka 3 koloko masana,*+ 45 popeza dzuwa linachita mdima. Pa nthawi imeneyi nsalu yotchinga+ ya m’nyumba yopatulika inang’ambika pakati+ kuchokera pamwamba mpaka pansi. 46 Pamenepo Yesu anafuula mokweza mawu kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu*+ wanga m’manja mwanu.” Atanena zimenezi anatsirizika.+ 47 Poona zochitikazo, kapitawo wa asilikali anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Ndithudi munthu uyu anali wolungama.”+ 48 Anthu onse amene anasonkhana kumeneko kudzaona zochitikazo, ataona zonse zimene zinachitika, anayamba kubwerera akudziguguda pachifuwa. 49 Komanso onse amene anali kumudziwa anaimirira chapatali ndithu.+ Ndipo amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anaimiriranso chapomwepo n’kumaonerera zinthu zimenezi.+
50 Tsopano panali mwamuna wina dzina lake Yosefe, amene anali wa m’Khoti Lalikulu la Ayuda, munthu wabwino ndi wolungama.+ 51 Munthu ameneyu sanavomereze chiwembu chawo ndi zochita zawo.+ Yosefe anali wochokera ku Arimateya, mzinda wa Ayudeya, ndipo anali kuyembekezera ufumu wa Mulungu.+ 52 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.+ 53 Choncho anautsitsa+ ndi kuukulunga munsalu yabwino kwambiri, kenako anakauika m’manda+ ogobedwa muthanthwe, mmene anali asanaikemo munthu chikhalire.+ 54 Tsopano linali Tsiku Lokonzekera,+ ndipo chisisira cha madzulo chosonyeza kuyambika kwa sabata+ chinali kuyambika. 55 Koma amayi amene anayenda limodzi ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anamutsatira kukaona manda achikumbutsowo+ ndi mmene mtembo wakewo anauikira.+ 56 Atatero anabwerera kukakonza zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira.+ Komabe pa tsiku la sabata+ anapuma malinga ndi chilamulo.
24 Pa tsiku loyamba la mlungu, amayi aja analawirira m’mawa kwambiri kupita kumandako, atatenga zonunkhira zimene anakonza zija.+ 2 Koma anapeza kuti mwala wagubuduzidwa pamanda achikumbutsowo,+ 3 ndipo atalowa m’mandamo, mtembo wa Ambuye Yesu sanaupezemo.+ 4 Atathedwa nzeru ndi zimenezi, anangoona amuna awiri ovala zovala zonyezimira ataima pambali pawo.+ 5 Amayiwo anagwidwa ndi mantha ndi kuweramira pansi. Ndiyeno amunawo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukufunafuna Munthu wamoyo pakati pa akufa? 6 [[Iye kuno kulibe, waukitsidwa.]]*+ Kumbukirani zimene anakuuzani pamene anali ku Galileya.+ 7 Paja ananena kuti Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m’manja mwa anthu ochimwa ndi kupachikidwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.”+ 8 Choncho anakumbukira mawu akewo.+ 9 Pamenepo anachoka kumanda achikumbutsowo n’kubwerera kukanena zonsezi kwa ophunzira 11 aja ndi kwa ena onse.+ 10 Amayiwa anali Mariya Mmagadala, Jowana+ ndi Mariya mayi wa Yakobo. Komanso amayi+ ena onse amene anali nawo pamodzi anali kuuza atumwi zinthu zimenezi. 11 Koma kwa iwo, zimene anali kuwauzazo zinali zopanda pake ndipo sanawakhulupirire amayiwo.+
12 [[Koma Petulo ananyamuka ndi kuthamangira kumanda achikumbutsoko, ndipo atasuzumira mkati, anangoona nsalu zokulungira mtembo zokha. Choncho anachoka ali wodabwa kwambiri ndi zimene zinachitikazo.]]
13 Koma tsiku lomweli, awiri a iwo anali pa ulendo wopita kumudzi wina wotchedwa Emau, pamtunda wa pafupifupi makilomita 11 kuchokera ku Yerusalemu. 14 Iwowa anali kukambirana zimene zinachitikazo.+
15 Tsopano ali mkati mokambirana ndi kufunsana, Yesu anafika+ ndi kuyamba kuyenda nawo limodzi. 16 Koma m’maso mwawo sanathe kumuzindikira.+ 17 Iye anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zanji zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?” Iwo anangoima chilili ndi nkhope zachisoni. 18 Poyankha, mmodzi dzina lake Keleopa anamufunsa kuti: “Kodi iwe ukukhala wekhawekha m’Yerusalemu monga mlendo, moti sukudziwa zimene zachitika mmenemo m’masiku amenewa?” 19 Iye anawafunsa kuti: “Zinthu zotani?” Iwo anamuuza kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti,+ amene anali mneneri+ wamphamvu m’ntchito ndi m’mawu pamaso pa Mulungu ndi anthu onse. 20 Komanso zokhudza mmene ansembe athu aakulu ndi olamulira anamuperekera ku chiweruzo cha imfa ndi kumupachika.+ 21 Komatu ife tinali kuyembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.+ Kuwonjezera pamenepo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni zinthu zimenezi. 22 Komanso amayi ena+ m’gulu lathu atidabwitsa kwambiri. Iwo analawirira m’mawa kwambiri kumanda achikumbutsoko, 23 koma mtembo wake sanaupeze. Anabwerako n’kumanena kuti aonanso masomphenya a angelo, amene awauza kuti iye ali ndi moyo. 24 Si zokhazo, enanso m’gulu lathu lomweli anapita kumanda achikumbutsoko,+ ndipo anapezadi kuti zili momwemo, mmene amayiwo ananenera, koma iyeyo sanamuone.”
25 Pamenepo iye anati: “Opanda nzeru inu ndi okayikakayika pa zonse zimene aneneri ananena!+ 26 Kodi sikunali kofunikira kuti Khristu amve zowawa+ zonsezi ndi kulowa mu ulemerero wake?”+ 27 Pamenepo anayamba kuwatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose+ ndi za aneneri zonse.+
28 Kenako anayandikira mudzi umene anali kupita, ndipo iye anachita ngati akupitirira ndi ulendo wake. 29 Koma iwo anamuumiriza kuti: “Tiyeni tikhalebe limodzi, chifukwa kunja kwayamba kuda ndipo tsiku latha kale.” Pamenepo analowa ndi kukakhala nawo. 30 Tsopano atakhala pansi n’kumadya nawo chakudya, anatenga mkate ndipo anaudalitsa, kuunyemanyema ndi kuwagawira.+ 31 Ataona izi, maso awo anatsegukiratu ndipo anamuzindikira, kenako iye anazimiririka.+ 32 Iwo anayamba kuuzana kuti: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mumsewu, ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?” 33 Pa ola lomwelo ananyamuka ndi kubwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anakapeza ophunzira 11 aja komanso ena amene anali nawo, atasonkhana pamodzi. 34 Iwo anawauza kuti: “N’zoonadi, Ambuye wauka kwa akufa ndipo waonekera kwa Simoni!”+ 35 Apa nawonso anafotokoza zimene zinachitika pamsewu ndi mmene iwo anamuzindikirira pamene ananyemanyema mkate.+
36 Akulankhula choncho Yesu anaimirira pakati pawo [[ndi kuwauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”]] 37 Koma iwo anaganiza kuti aona mzimu, ndipo anadzidzimuka kwambiri ndi kuchita mantha.+ 38 Koma iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuvutika maganizo? Bwanji mukukayikakayika m’mitima yanu? 39 Onani manja ndi mapazi angawa, mutsimikize kuti ndine ndithu. Ndikhudzeni muone,+ chifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa+ ngati anga amene mukuwaonawa.” 40 [[Pamene anali kunena zimenezi, anawaonetsa manja ndi mapazi ake.]] 41 Koma iwo, pokhalabe osakhulupirira+ chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”+ 42 Anamupatsa chidutswa cha nsomba yowotcha,+ 43 ndipo iye analandira ndi kudya+ onse akuona.
44 Ndiyeno anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi+ ndinakuuzani mawu akuti, zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri+ ndi m’Masalimo+ ziyenera kukwaniritsidwa.” 45 Pamenepo anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.+ 46 Kenako anawauza kuti: “Mmene zachitikiramu ndi mmene zinalembedwera kuti Khristu adzazunzika ndi kuuka kwa akufa tsiku lachitatu,+ 47 ndipo pa maziko a dzina lake, m’mitundu yonse+ mudzalalikidwa za kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ Kuyambira ku Yerusalemu+ 48 inu mudzakhala mboni+ za zimenezi. 49 Ndipo ine ndidzatumiza kwa inu chimene Atate wanga analonjeza. Koma inu mukhalebe mumzindawu kufikira mutalandira mphamvu zochokera kumwamba.”+
50 Pamenepo anawatsogolera kupita nawo ku Betaniya. Kumeneko anakweza manja ake ndi kuwadalitsa.+ 51 Pamene anali kuwadalitsa choncho, analekana nawo, ndi kuyamba kukwera kumwamba.+ 52 Pamenepo anamugwadira ndi kubwerera ku Yerusalemu ali ndi chimwemwe chochuluka.+ 53 Nthawi zonse iwo anali m’kachisi kutamanda Mulungu.+
Onani mawu a m’munsi pa Mt 2:1.
Kapena kuti “mpulumutsi wamphamvu.” Kawirikawiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti nyanga monga chizindikiro cha nyonga, mphamvu, kapena ulamuliro.
Onani Zakumapeto 2.
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Dzina limene talimasulira pano kuti “Yesu,” mipukutu ina yakale imati “Yose.”
Onani Zakumapeto 2.
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
M’Baibulo, “nyanja ya Genesarete” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Galileya, komanso nyanja ya Tiberiyo.
Kapena kuti “patsindwi.”
Mawu ake enieni, “Wobwerayo.”
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
Onani Zakumapeto 9.
Mawu ake enieni, “za kuchoka kwake kumene iye anayenera kudzakwaniritsa ku Yerusalemu.”
Onani Zakumapeto 5.
Onani mawu a m’munsi pa Mt 6:12.
“Belezebule” ndi dzina lina la Satana.
Onani Zakumapeto 6.
Mawu ake enieni, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.”
Mawu amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:25.
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakang’ono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita anayi ndipo kamachita nthambi.
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
Kutanthauza kachisi.
Onani Zakumapeto 9.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Onani Zakumapeto 9.
Mikutiramawu yophatikiza ikusonyeza mawu amene mulibe m’mipukutu ina yakale koma akupezeka m’mipukutu ina.
Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Onani Zakumapeto 4.
Onani mawu a m’munsi pa Lu 23:34.