Yohane
1 Pa chiyambi,+ panali wina wotchedwa Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu,+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+ 2 Ameneyu anali ndi Mulungu+ pa chiyambi.+ 3 Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye,+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.
4 Moyo unakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo moyowo unali kuwala+ kounikira anthu. 5 Kuwalako kukuunika mumdima,+ ndipo mdimawo sunagonjetse kuwalako.
6 Panaonekera munthu wina amene anatumidwa monga nthumwi ya Mulungu.+ Dzina lake anali Yohane.+ 7 Munthu ameneyu anabwera monga mboni,+ kudzachitira umboni za kuwala,+ kuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.+ 8 Sikuti iyeyu anali kuwalako ayi,+ koma anangobwera kudzachitira umboni+ za kuwalako.
9 Kuwala+ kwenikweni kumene kumaunikira+ anthu osiyanasiyana+ kunali pafupi kubwera m’dziko. 10 Iye anali m’dziko,+ ndipo dziko linakhalapo kudzera mwa iye.+ Koma dzikolo silinamudziwe. 11 Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanamulandire.+ 12 Komabe onse amene anamulandira,+ anawapatsa mphamvu zokhala ana a Mulungu,+ chifukwa amenewa anakhulupirira m’dzina lake.+ 13 Iwowa anabadwa kwa Mulungu, osati kudzera m’magazi kapena m’chifuniro cha thupi, kapena chifuniro cha anthu.+
14 Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi+ la nyama ndi kukhala pakati pathu, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wa mwana wobadwa yekha+ kwa bambo ake. Anali wodzaza ndi kukoma mtima kwakukulu ndi choonadi.+ 15 (Yohane anachitira umboni za iye, moti anali kuchita kufuula kuti: “Amene akubwera m’mbuyo mwangamu wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.”)+ 16 Pakuti tonsefe tinalandira zinthu kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo.+ Tinalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira.+ 17 Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi+ zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu. 18 Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse,+ mulungu wobadwa yekha+ amene ali pachifuwa+ cha Atate ndiye amene anafotokoza za Mulungu.+
19 Tsopano, Yohane anapereka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kuchokera ku Yerusalemu kukamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?”+ 20 Iye anavomereza osakana ayi. Anavomereza ndithu, kuti: “Ine sindine Khristu ayi.”+ 21 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Koma iye anati: “Iyayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!” 22 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Ndiwe ndani nanga? Tikufuna kudziwa kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?”+ 23 Iye anati: “Ndine mawu a winawake wofuula m’chipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”+ 24 Otumidwawo anachokera kwa Afarisi. 25 Choncho anamufunsa kuti: “Ngati iweyo sindiwe Khristu, kapena Eliya, kapenanso Mneneri, nanga n’chifukwa chiyani umabatiza anthu?”+ 26 Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza m’madzi. Pakati panu+ paimirira wina amene inu simukumudziwa.+ 27 Iye ndiye amene akubwera m’mbuyo mwangamu. Komabe, zingwe za nsapato zake ine sindili woyenera kuzimasula.”+ 28 Izi zinachitikira ku Betaniya wa kutsidya lina la Yorodano, kumene Yohane anali kubatiza anthu.+
29 Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+ 30 Uyu ndi amene ndinali kunena uja kuti, M’mbuyo mwanga mukubwera munthu wina amene wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.+ 31 Inenso sindinali kumudziwa, koma chimene ndikubatizira anthu m’madzi n’chakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”+ 32 Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba, ndipo unakhalabe pa iye.+ 33 Inenso sindinali kumudziwa, koma Amene anandituma+ kudzabatiza m’madzi anandiuza kuti, ‘Ukadzaona mzimu ukutsika ndi kukhazikika pa munthu wina, ameneyo ndiye wobatiza ndi mzimu woyera.’+ 34 Ndipo ine ndaonadi zimenezo, ndachitira umboni ndithu kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+
35 Tsiku lotsatiranso Yohane anaimirira ndi ophunzira ake awiri. 36 Poyang’anitsitsa Yesu akuyenda iye anati: “Onani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu!” 37 Ophunzira awiriwo anamumva akulankhula, ndipo anatsatira Yesu. 38 Pamenepo Yesu anacheuka. Atawaona akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?” Iwo anati: “Rabi, (dzina lotanthauza, Mphunzitsi, polimasulira,) kodi mukukhala kuti?” 39 Iye anati: “Tiyeni mukaoneko.”+ Choncho anapita ndi kukaona kumene anali kukhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Pamenepo n’kuti nthawi ili cha m’ma 4 koloko madzulo.* 40 Andireya+ m’bale wake wa Simoni Petulo, anali mmodzi wa awiriwo amene anamva zimene Yohane ananena ndi kutsatira Yesu. 41 Choyamba iyeyu anapeza m’bale wake Simoni, ndi kumuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”+ (dzina lotanthauza, Khristu,+ polimasulira). 42 Kenako iye anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuyang’ana+ anati: “Iwe ndiwe Simoni+ mwana wa Yohane,+ udzatchedwa Kefa” (dzina limene kumasulira kwake ndi Petulo).+
43 Tsiku lotsatira, Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Ndiyeno anapeza Filipo+ n’kumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ 44 Filipo anali wochokera ku Betsaida,+ mumzinda wa Andireya ndi Petulo. 45 Kenako Filipo anapeza Natanayeli+ n’kumuuza kuti: “Uja amene Mose analemba za iye m’Chilamulo+ komanso wotchulidwa m’Zolemba za aneneri,+ ife tam’peza. Iyeyu ndi Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti.” 46 Koma Natanayeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?”+ Pamenepo Filipo anati: “Tiye ukaone.” 47 Yesu ataona Natanayeli akubwera momulunjika anati: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”+ 48 Natanayeli anati: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona, muja unali pansi pa mkuyu paja.” 49 Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinudi Mwana wa Mulungu,+ ndinu Mfumu+ ya Isiraeli.” 50 Poyankha Yesu anati: “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mkuyu? Udzaona zazikulu kuposa izi.” 51 Anamuuzanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo+ a Mulungu akukwera ndi kutsikira kwa Mwana wa munthu.”+
2 Tsopano tsiku lachitatu kunali phwando la ukwati ku Kana+ ku Galileya. Mayi+ a Yesu analinso komweko. 2 Yesunso ndi ophunzira ake anaitanidwa ku phwando la ukwatilo.
3 Vinyo atatha, mayi+ a Yesu anamuuza kuti: “Vinyo waathera.” 4 Koma Yesu anauza mayi akewo kuti: “Kodi ndili nanu chiyani mayi?+ Nthawi yanga sinafike.”+ 5 Mayi akewo anauza amene anali kutumikira kuti: “Chilichonse chimene angakuuzeni, chitani chimenecho.”+ 6 Pamalopo panali mbiya zamwala zokwanira 6 malinga ndi malamulo a Ayuda a kudziyeretsa.+ Mbiya iliyonse inali ya malita pafupifupi 44 mpaka 66. 7 Choncho Yesu anawauza kuti: “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Iwo anazidzazadi mpaka pakamwa. 8 Ndiyeno anawauza kuti: “Tunganimo tsopano mupereke kwa woyang’anira phwandoli.” Iwo anaperekadi. 9 Tsopano woyang’anira phwando analawa madzi amene anawasandutsa vinyowo.+ Iye sanadziwe kumene wachokera, ngakhale kuti otumikira amene anatunga madziwo anadziwa. Atatero woyang’anira phwando uja anaitana mkwati 10 ndi kumuuza kuti: “Munthu aliyense amatulutsa vinyo wabwino choyamba,+ ndipo anthu akaledzera, m’pamene amatulutsa wosakoma kwenikweni. Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.” 11 Yesu anachita zimenezi ku Kana mu Galileya monga chiyambi cha zizindikiro zake. Pamenepo anaonetsa ulemerero wake,+ ndipo ophunzira ake anakhulupirira mwa iye.
12 Izi zitatha, iye, mayi ake, abale ake+ ndi ophunzira ake anapita ku Kaperenao,+ koma kumeneko sanakhaleko masiku ambiri.
13 Tsopano pasika+ wa Ayuda anali pafupi. Choncho Yesu ananyamuka kupita ku Yerusalemu.+ 14 Kumeneko anapeza ogulitsa ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda+ komanso osintha ndalama ali m’kachisi atakhala m’mipando yawo. 15 Choncho anapanga mkwapulo wazingwe, n’kuthamangitsa onse amene anali ndi nkhosa ndi ng’ombe ndipo anawatulutsa m’kachisimo. Anakhuthula makobidi a osintha ndalama ndi kugubuduza matebulo awo.+ 16 Tsopano anauza ogulitsa nkhundawo kuti: “Chotsani izi muno! Mulekeretu kusandutsa nyumba+ ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!”+ 17 Pamenepo ophunzira ake anakumbukira zimene Malemba amanena, kuti amati: “Kudzipereka kwambiri panyumba yanu kudzandidya.”+
18 Koma Ayudawo anati: “Utionetsa chizindikiro+ chotani tsopano chosonyeza kuti uli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi?” 19 Yesu anawayankha kuti: “Gwetsani kachisi uyu,+ ndipo ine ndidzamumanga m’masiku atatu.” 20 Pamenepo Ayudawo anati: “Kachisi ameneyu anamumanga zaka 46, ndiye iwe udzamumanga m’masiku atatu?” 21 Komatu iye anali kunena za kachisi+ wa thupi lake. 22 Choncho pamene anauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira+ kuti anali kunena zimenezi, ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu ananena.
23 Tsopano pamene anali mu Yerusalemu pa chikondwerero+ cha pasika, anthu ambiri anakhulupirira m’dzina lake,+ ataona zizindikiro zimene anali kuchita.+ 24 Koma Yesu sanawakhulupirire+ kwenikweni chifukwa onsewo anali kuwadziwa. 25 Komanso, iye sanafunikire wina woti achite kumuuza za munthu, chifukwa payekha anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.+
3 Tsopano panali Mfarisi wina dzina lake Nikodemo,+ wolamulira wa Ayuda. 2 Iyeyu anabwera kwa Yesu usiku+ ndi kumuuza kuti: “Rabi,+ tikudziwa kuti inu ndinu mphunzitsi+ wochokera kwa Mulungu,+ chifukwa munthu sangathe kuchita zizindikiro+ zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.”+ 3 Poyankha Yesu anati:+ “Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.”+ 4 Nikodemo anafunsa kuti: “Munthu angabadwe bwanji ali wamkulu kale? Kodi angathe kulowa m’mimba mwa mayi ake ndi kubadwanso?” 5 Yesu anayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi+ ndi mzimu.+ 6 Chobadwa mwa thupi n’chanyama, ndipo chobadwa mwa mzimu n’chauzimu.+ 7 Usadabwe chifukwa ndakuuza kuti, Anthu inu muyenera kubadwanso.+ 8 Mphepo+ imawombera kumene ikufuna, ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. N’chimodzimodzinso aliyense wobadwa mwa mzimu.”+
9 Poyankha Nikodemo anati: “Zimenezi zingatheke bwanji?” 10 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi iwe sudziwa zinthu zimenezi, chikhalirecho ndiwe mphunzitsi wa Isiraeli?+ 11 Ndithudi ndikukuuza, Zimene ife timadziwa timazilankhula, ndipo zimene taona timazichitira umboni.+ Koma anthu inu simulandira umboni umene timapereka.+ 12 Ngati ndakuuzani zinthu za padziko lapansi koma inu osakhulupirira, mudzakhulupirira bwanji ndikakuuzani zinthu zakumwamba?+ 13 Ndipo palibe munthu amene anakwera kumwamba+ koma Mwana wa munthu+ yekha, amene anatsika kuchokera kumwambako.+ 14 Ndiponso, monga mmene Mose anakwezera njoka m’mwamba+ m’chipululu, momwemonso Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa m’mwamba,+ 15 kuti aliyense wokhulupirira iye akhale nawo moyo wosatha.+
16 “Pakuti Mulungu anakonda+ kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha,+ kuti aliyense wokhulupirira+ iye asawonongeke,+ koma akhale ndi moyo wosatha.+ 17 Pakuti Mulungu anatumiza Mwana wake m’dziko, osati kuti mwanayo adzaweruze+ dziko, koma kuti mwa iye, dziko lipulumutsidwe.+ 18 Wokhulupirira mwa iye sayenera kuweruzidwa.+ Wosakhulupirira waweruzidwa kale, chifukwa sanakhulupirire m’dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.+ 19 Tsopano maziko operekera chiweruzo ndi awa, kuwala+ kwafika m’dziko+ koma anthu akonda mdima m’malo mwa kuwala,+ pakuti ntchito zawo n’zoipa. 20 Amene amachita zinthu zoipa+ amadana ndi kuwala ndipo safika pamene pali kuwala, kuti ntchito zake zisadzudzulidwe.+ 21 Koma amene amachita chimene chili chabwino amabwera pamene pali kuwala,+ kuti ntchito zake zionekere kuti anazichita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.”
22 Izi zitatha, Yesu ndi ophunzira ake anapita m’dera la Yudeya, ndipo anakhala nawo kumeneko ndi kubatiza anthu.+ 23 Koma Yohane+ analinso kubatiza ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kunali madzi ambiri+ kumeneko, ndipo anthu anali kubwera kudzabatizidwa.+ 24 Pa nthawiyi n’kuti Yohane asanaponyedwe m’ndende.+
25 Tsopano ophunzira a Yohane anayambitsa mkangano ndi Myuda wina pa nkhani yokhudza mwambo wa kuyeretsa.+ 26 Pamenepo anafika kwa Yohane ndi kumuuza kuti: “Rabi, munthu amene munali naye kutsidya kwa Yorodano uja, amene munali kumuchitira umboni uja,+ iyenso akubatiza ndipo anthu onse akupita kwa iye.”+ 27 Poyankha Yohane anati: “Munthu sangalandire kanthu kalikonse akapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba.+ 28 Inu nomwe ndinu mboni zanga pamawu amene ndinanena kuti, Ine sindine Khristu,+ koma, ndinatumizidwa monga kalambulabwalo wake.+ 29 Iye amene ali ndi mkwatibwi ndiye mkwati.+ Koma mnzake wa mkwati, akaimirira ndi kumvetsera zimene akunena, amakhala n’chimwemwe chochuluka chifukwa cha mawu a mkwatiyo. Choncho chimwemwe changa chasefukiradi.+ 30 Ameneyo ayenera kumawonjezereka, koma ine ndiyenera kucheperachepera.”
31 Wochokera kumwamba ali woposa ena onse.+ Wochokera padziko lapansi ndi wa padziko lapansi, ndipo amalankhula zinthu za padziko lapansi.+ Koma wochokera kumwamba ali woposa ena onse.+ 32 Zimene iye waziona ndi kuzimva, akuchitira umboni zimenezo,+ koma palibe munthu amene akulandira umboni wake.+ 33 Amene walandira umboni wakewo waika chisindikizo chake pa umboniwo chakuti Mulungu amanena zoona.+ 34 Wotumidwa ndi Mulungu amalankhula mawu a Mulungu,+ pakuti akafuna kupereka mzimu sachita kuyeza pamuyezo.+ 35 Atate amakonda Mwana wake+ ndipo anapereka zinthu zonse m’manja mwake.+ 36 Iye wokhulupirira+ mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.+ Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu,+ koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.+
4 Tsopano Ambuye atazindikira kuti Afarisi anamva kuti Yesu anali kuphunzitsa anthu ambiri kuposa Yohane ndipo anali kuwabatiza+ kuti akhale ophunzira, 2 ngakhale kuti kwenikweni si Yesu amene anali kubatiza koma ophunzira ake, 3 anachoka ku Yudeya ndi kupitanso ku Galileya. 4 Koma anafunika kuti adzere ku Samariya.+ 5 Choncho anafika mumzinda wa Samariya wotchedwa Sukari pafupi ndi munda umene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.+ 6 Ndipotu kumeneko kunali kasupe+ wa Yakobo. Yesu atatopa ndi ulendowo, anakhala pansi pakasupepo. Nthawi n’kuti ili cha m’ma 12 koloko masana.*
7 Ndiyeno mayi wina wa mu Samariya anafika kudzatunga madzi. Yesu anapempha mayiyo kuti: “Mundipatseko madzi akumwa mayi.” 8 (Ophunzira ake anali atalowa mumzinda kukagula chakudya.) 9 Mayi wachisamariyayo anafunsa Yesu kuti: “Popeza inu ndinu Myuda, bwanji mukupempha madzi akumwa kwa ine, mayi wachisamariya?” (Pakuti Ayuda ndi Asamariya sayanjana.)+ 10 Poyankha Yesu anauza mayiyo kuti: “Mukanadziwa mphatso+ yaulere ya Mulungu ndi amene+ akukuuzani kuti, ‘Mundipatseko madzi akumwa,’ mukanam’pempha iyeyo, ndipo akanakupatsani madzi amoyo.”+ 11 Mayiyo anati: “Bambo, mulibe n’chotungira chomwe, ndipo chitsimechinso n’chozama. Nanga madzi amoyowo mwawatenga kuti? 12 Kodi inu ndinu wamkulu+ kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi, chimenenso iyeyo, ana ake ndi ng’ombe zake anali kumwa?” 13 Poyankha, Yesu anamuuza kuti: “Aliyense wakumwa madzi awa adzamvanso ludzu. 14 Koma amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu m’pang’ono pomwe.+ Ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi+ otuluka mwa iye, opatsa moyo wosatha.”+ 15 Mayiyo anauza Yesu kuti: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo, kuti ndisadzamvenso ludzu komanso kuti ndisamabwerenso kuno kudzatunga madzi.”
16 Iye anauza mayiyo kuti: “Pitani, kaitaneni mwamuna wanu abwere kuno.” 17 Mayiyo anayankha kuti: “Ndilibe mwamuna.” Yesu anati: “Mwanena zoona mmene mukuti, ‘Ndilibe mwamuna.’ 18 Pakuti mwakwatiwapo ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye panopa si mwamuna wanu. Apa mwanenadi zoona.” 19 Mayiyo anati: “Bambo, ndazindikira kuti ndinu mneneri.+ 20 Makolo athu anali kulambira m’phiri ili,+ koma anthu inu mumanena kuti Yerusalemu ndiwo malo kumene anthu ayenera kulambirirako.”+ 21 Yesu anauza mayiyo kuti: “Mayi, Ndithu nthawi idzafika pamene anthu inu simudzalambira+ Atate m’phiri ili kapena ku Yerusalemu.+ 22 Inu mumalambira chimene simuchidziwa.+ Ife timalambira chimene tikuchidziwa, chifukwa chipulumutso chikuchokera kwa Ayuda.+ 23 Komabe nthawi idzafika, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu+ ndi choonadi,+ pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.+ 24 Mulungu ndiye Mzimu,+ ndipo onse omulambira ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”+ 25 Pamenepo mayiyo anati: “Ndikudziwa kuti Mesiya+ akubwera, wotchedwa Khristu.+ Ameneyo akadzafika, adzatifotokozera zonse poyera.” 26 Yesu anamuuza kuti: “Munthu ameneyo ndi ineyo amene ndikulankhula nanu.”+
27 Tsopano ophunzira ake anafika, ndipo anayamba kudabwa chifukwa anali kulankhula ndi munthu wamkazi. Komabe palibe amene ananena kuti: “Mukufuna chiyani kwa iye?” kapena kuti, “N’chifukwa chiyani mukulankhula ndi mayiyu?” 28 Choncho mayi uja anasiya mtsuko wake wa madzi ndi kukalowa mumzinda ndipo anauza anthu kuti: 29 “Tiyeni kuno mukaone munthu amene wandiuza zonse zimene ndakhala ndikuchita. Kodi ameneyu n’kukhala Khristu+ kapena?” 30 Iwo anatuluka mumzindawo ndi kubwera kumene kunali Yesu.
31 Apa n’kuti ophunzira ake akumupempha kuti: “Rabi,+ idyani.” 32 Koma iye anawauza kuti: “Chakudya ndili nacho chimene inu simukuchidziwa.” 33 Pamenepo ophunzirawo anayamba kufunsana kuti: “Pali amene wamubweretsera chakudya ngati?” 34 Yesu anati: “Chakudya+ changa ndicho kuchita chifuniro+ cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.+ 35 Kodi inu simunena kuti kwatsala miyezi inayi kuti tiyambe kukolola? Koma ndikuti: Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.+ Moti pano 36 wokolola akulandira kale malipiro ndipo akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha,+ kuti wofesa mbewu+ ndi wokolola asangalalire pamodzi.+ 37 Ndiye chifukwa chake mawu aja ali oona akuti, Wina ndi wofesa ndipo wina ndi wokolola. 38 Ine ndakutumizani kukakolola zimene simunakhetsere thukuta. Ena anagwira ntchito mwakhama,+ ndipo inu mwalowa kukapindula ndi ntchito imene iwo anaigwira mwamphamvu.”
39 Pamenepo Asamariya ambiri ochokera mumzindawo anakhulupirira+ mwa iye chifukwa cha mawu a mayi uja amene pochitira umboni anati: “Iyeyu anandiuza zinthu zonse zimene ndakhala ndikuchita.”+ 40 Choncho Asamariya atafika kwa iye, anayamba kumupempha kuti akhalebe nawo, ndipo anakhala nawo masiku awiri.+ 41 Zotsatira zake, anthu ochuluka anakhulupirira chifukwa cha zimene iye anali kunena.+ 42 Iwo anayamba kuuza mayi uja kuti: “Sikuti tikukhulupirira chifukwa cha mawu ako ajanso ayi, pakuti tadzimvera tokha+ ndipo tadziwa ndithu kuti munthu uyu ndi mpulumutsi+ wa dziko.”
43 Masiku awiriwo atatha, iye anachoka kumeneko ndi kupita ku Galileya.+ 44 Yesu mwiniyo anachitira umboni kuti mneneri salemekezedwa kwawo.+ 45 Choncho pamene anafika ku Galileya, Agalileyawo anamulandira, chifukwa anali ataona zonse zimene anachita pa chikondwerero ku Yerusalemu,+ pakuti nawonso anapita ku chikondwereroko.+
46 Kenako anafikanso ku Kana+ wa ku Galileya, kumene anasandutsa madzi kukhala vinyo kuja.+ Tsopano kumeneku kunali munthu wina mtumiki wa mfumu, amene mwana wake wamwamuna anali kudwala ku Kaperenao.+ 47 Munthuyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa iye ndi kuyamba kumupempha kuti apiteko ndi kukachiritsa mwana wakeyo, pakuti anali pafupi kumwalira. 48 Koma Yesu anamuuza kuti: “Ngati anthu inu simunaone zizindikiro+ ndi zodabwitsa,+ simungakhulupirire ngakhale pang’ono.” 49 Mtumiki wa mfumu uja anati: “Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.” 50 Yesu anati: “Pita,+ mwana wako ali moyo.”+ Munthuyo anakhulupirira mawu amene Yesu anamuuzawo ndipo anapitadi. 51 Ali m’njira, akapolo ake anamuchingamira kudzamuuza kuti mnyamata wake ali moyo.+ 52 Choncho iye anayamba kuwafunsa ola limene anachira. Iwo anamuuza kuti: “Malungo* ake anatha dzulo cha m’ma 1 koloko masana.”*+ 53 Pamenepo bamboyo anadziwa kuti linali ola lomwelo+ pamene Yesu anamuuza kuti: “Mwana wako ali moyo.” Ndipo iye ndi banja lake lonse anakhulupirira.+ 54 Ichi chinalinso chizindikiro+ chachiwiri chimene Yesu anachita atatuluka mu Yudeya ndi kulowa mu Galileya.
5 Pambuyo pa zonsezi, kunali chikondwerero+ cha Ayuda, ndipo Yesu ananyamuka kupita ku Yerusalemu. 2 Tsopano mu Yerusalemu pachipata cha nkhosa+ pali dziwe limene m’Chiheberi limatchedwa Betesida. M’mbali mwa dziwelo muli makonde asanu amene ali ndi zipilala. 3 Mmenemu munagona anthu ambiri odwala, akhungu, olumala ndi ena opuwala ziwalo. 4* —— 5 Pamenepo panalinso mwamuna wina amene anakhala akudwala zaka 38. 6 Ataona munthu ameneyu ali chigonere, komanso podziwa kuti wakhala akudwala nthawi yaitali,+ Yesu anamufunsa kuti: “Kodi ukufuna kuchira?”+ 7 Wodwalayo anamuyankha kuti: “Bambo, ndilibe munthu wondiviika m’dziwemu madzi akawinduka, ndipo ndikati ndikalowemo wina amandipitirira n’kulowamo.” 8 Yesu anati: “Nyamuka, nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.”+ 9 Nthawi yomweyo munthu uja anachira. Pamenepo ananyamula machira akewo n’kuyamba kuyenda.
Komano limenelo linali tsiku la sabata.+ 10 Choncho Ayuda anayamba kuuza munthu wochiritsidwa uja kuti: “Lero ndi Sabata, n’kosaloleka+ kuti unyamule machirawa.” 11 Iye anawayankha kuti: “Amene wandichiritsayo wandiuza kuti, ‘Nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.’” 12 Iwo anamufunsa kuti: “Ndiye ndani amene wakuuza kuti, ‘Nyamula machira ndi kuyamba kuyenda’?” 13 Koma munthu wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anali atalowa m’chikhamu cha anthu amene anali pamalopo.
14 Kenako Yesu anapeza munthu uja m’kachisi ndi kumuuza kuti: “Onatu wachira tsopano. Usakachimwenso, kuti chinachake choopsa kuposa matenda chisadzakuchitikire.” 15 Munthu uja anachoka ndi kukauza Ayuda aja kuti Yesu ndi amene wamuchiritsa. 16 Atamva zimenezi Ayudawo anayamba kuvutitsa+ Yesu, chifukwa anali kuchita zinthu zimenezi pa Sabata. 17 Koma iye anawauza kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.”+ 18 Pa chifukwa chimenechi, Ayudawo anayamba kufunafuna njira yomuphera,+ chifukwa kuwonjezera pa kuphwanya Sabata, anali kunenanso kuti Mulungu ndi Atate wake,+ kudziyesa wofanana+ ndi Mulungu.
19 Ndipo Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mwanayo sangachite chilichonse chongoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.+ Pakuti zilizonse zimene Atatewo amachita, Mwana amachitanso zomwezo. 20 Atatewo amakonda Mwana wake.+ Amamuonetsa zonse zimene iwo akuchita, ndipo adzamuonetsa ntchito zazikulu kuposa izi, kuti inu mudabwe.+ 21 Pakuti monga Atate amaukitsa akufa ndi kuwapatsa moyo,+ nayenso Mwana amapereka moyo kwa amene iye wafuna kuwapatsa.+ 22 Atate saweruza munthu aliyense, koma wapereka udindo wonse woweruza kwa Mwana,+ 23 kuti onse alemekeze Mwana+ monga mmene amalemekezera Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamutuma.+ 24 Ndithudi ndikukuuzani, Iye wakumva mawu anga ndi kukhulupirira amene anandituma ine ali nawo moyo wosatha,+ ndipo salowa m’chiweruzo koma wachoka ku imfa, waolokera ku moyo.+
25 “Ndithudi ndikukuuzani, Nthawi idzafika, ndipo ndi inoyi, pamene akufa+ adzamva mawu+ a Mwana wa Mulungu, ndipo olabadirawo adzakhala ndi moyo.+ 26 Pakuti monga Atate ali nawo moyo mwa iwo wokha,+ alolanso Mwana kukhala nawo moyo mwa iye yekha.+ 27 Amupatsanso mphamvu zoweruza,+ chifukwa iye ndi Mwana wa munthu.+ 28 Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso+ adzamva mawu ake 29 ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo.+ Amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.+ 30 Ine sindingachite chilichonse chongoganiza ndekha. Ndimaweruza malinga ndi mmene ndamvera, ndipo chiweruzo chimene ndimapereka n’cholungama,+ chifukwa sinditsatira chifuniro changa, koma chifuniro+ cha amene anandituma.
31 “Ngati ndidzichitira umboni+ ine ndekha, ndiye kuti umboni wanga suli woona.+ 32 Alipo wina amene akuchitira umboni za ine, ndipo ndikudziwa kuti umboni umene akundichitirawo+ ndi woona. 33 Inu munatumiza anthu kwa Yohane, ndipo iye anachitira umboni choonadi.+ 34 Komatu ine sindivomereza umboni wochokera kwa munthu, koma ndikunena izi kuti inu mupulumuke.+ 35 Munthu ameneyu anali nyale yoyaka ndi yowala, ndipo kwa kanthawi kochepa inu munali ofunitsitsa kusangalala m’kuwala kwakeko.+ 36 Koma ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane, pakuti ntchito zenizenizo zimene Atate wanga anandipatsa kuti ndizikwaniritse, ntchito zimene ine ndikuchita,+ zikundichitira umboni kuti Atate ananditumadi. 37 Komanso Atate amene anandituma andichitira umboni.+ Inu simunamvepo mawu ake nthawi ina iliyonse, kapena kuona thupi lake.+ 38 Mawu akenso sanakhazikike mwa inu, chifukwa simukhulupirira amene Atatewo anamutumiza.
39 “Inu mumafufuza m’Malemba,+ chifukwa mumaganiza kuti kudzera m’Malembawo mudzapeza moyo wosatha, ndipo Malemba omwewo ndi amenenso amachitira umboni za ine.+ 40 Koma simufuna kubwera kwa ine kuti mupeze moyo.+ 41 Sindikufuna ulemerero wochokera kwa anthu,+ 42 koma ndikudziwa bwino ndithu kuti mwa inu mulibe chikondi cha Mulungu.+ 43 Ndabwera m’dzina la Atate wanga,+ ndipo simunandilandire, koma wina akanabwera m’dzina lake, mukanamulandira ameneyo. 44 Mungakhulupirire bwanji, pamene mumalandira ulemerero+ kuchokera kwa anthu anzanu, koma osayesetsa kupeza ulemerero wochokera kwa Mulungu yekhayo?+ 45 Musaganize kuti ine ndikunenezani kwa Atate. Alipo amene amakunenezani, ndiye Mose+ amene munaika chiyembekezo chanu mwa iye. 46 Ndipo ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso ine, pakuti iyeyo analemba za ine.+ 47 Koma ngati simukhulupirira zolemba za ameneyo,+ mungakhulupirire bwanji mawu anga?”
6 Tsopano Yesu anawolokera kutsidya lina la nyanja ya Galileya,* kapena kuti nyanja ya Tiberiyo.+ 2 Koma khamu lalikulu la anthu linali kumutsatira, chifukwa linali kuona zizindikiro zimene iye anali kuchita pa odwala.+ 3 Choncho Yesu anakwera m’phiri.+ Kumeneko anakhala pansi pamodzi ndi ophunzira ake. 4 Tsopano chikondwerero cha Ayuda cha pasika+ chinayandikira. 5 Ndiyeno Yesu atakweza maso ake ndi kuona khamu lalikulu la anthu likubwera kwa iye, anafunsa Filipo kuti: “Kodi mitanda ya mkate yodyetsa anthu onsewa tikaigula kuti?”+ 6 Komatu iye ananena izi mongomuyesa, popeza anali atadziwa kale chimene ati achite. 7 Filipo anamuyankha kuti: “Ngakhale mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari 200 singawakwanire amenewa. Singawakwanire ngakhale titati aliyense angolandirako pang’ono.”+ 8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andireya m’bale wake wa Simoni Petulo, anati: 9 “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda isanu ya mkate wa balere+ ndi tinsomba tiwiri. Koma nanga zimenezi zingakwanire, poyerekeza ndi chikhamu chonse cha anthuchi?”+
10 Yesu ananena kuti: “Akhazikeni pansi anthuwa muja amakhalira pa chakudya.”+ Pamalopo panali udzu wambiri. Choncho amuna pafupifupi 5,000 anakhaladi pansi.+ 11 Ndiyeno Yesu anatenga mitanda ya mkate ija. Atayamika, anaigawira kwa anthu onse amene anakhala pansi aja. Chimodzimodzinso ndi tinsomba tija, anatigawira kwa anthuwo mmene aliyense anafunira.+ 12 Anthu onsewo atakhuta,+ iye anauza ophunzira ake kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.” 13 Choncho anatolera zonse, ndipo zinadzaza madengu 12 kuchokera pa mitanda ya mkate wa balere isanu ija, imene onse anadya ndi kuilephera.+
14 Tsopano anthuwo ataona zizindikiro zimene anachitazo, anayamba kunena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri+ uja amene anati adzabwera padziko.” 15 Choncho Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kumugwira kuti amuveke ufumu, anachoka+ ndi kupitanso kuphiri yekhayekha.
16 Chakumadzulo ndithu, ophunzira ake anapita kunyanja.+ 17 Iwo anakwera ngalawa ndi kuyamba kuwoloka nyanja kulowera ku Kaperenao. Pa nthawiyi n’kuti mdima utagwa ndipo Yesu anali asanabwerebe kwa iwo. 18 Komanso nyanja inayamba kuwinduka chifukwa panali kuwomba mphepo yamphamvu.+ 19 Koma atapalasa makilomita pafupifupi 5 kapena 6, anaona Yesu akuyenda panyanja, kuyandikira ngalawayo ndipo iwo anachita mantha.+ 20 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ndine, musachite mantha!”+ 21 Pamenepo anamulandira m’ngalawa yawo, ndipo posapita nthawi ngalawa ija inakaima kumtunda kumene anali kupita.+
22 Tsiku lotsatira, anthu amene anaima kutsidya lina la nyanjayo anaona kuti ngalawa ina palibe koma pali imodzi yokha yaing’ono. Choncho anadziwa kuti Yesu sanakwere ngalawa pamodzi ndi ophunzira ake koma kuti ophunzira akewo anachoka paokha. 23 Ngalawa zochokera ku Tiberiyo zinafika pafupi ndi pamalo amene anthuwo anadyera mkate uja Ambuye atayamika. 24 Ndiyeno khamu la anthulo litaona kuti Yesu komanso ophunzira ake kulibe, linakwera ngalawa zawo zing’onozing’ono ndi kupita ku Kaperenao kukafunafuna+ Yesu.
25 Atamupeza kutsidya kwa nyanjayo anamufunsa kuti: “Rabi,+ mwafika nthawi yanji kuno?” 26 Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mukundifunafuna osati chifukwa munaona zizindikiro ayi, koma chifukwa munadya mikate ndi kukhuta.+ 27 Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka,+ koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha,+ chimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate, Mulungu yekhayo, waika chisindikizo pa iye chomuvomereza.”+
28 Pamenepo iwo anati: “Tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?” 29 Yesu anawauza kuti: “Ntchito ya Mulungu ndi iyi, musonyeze chikhulupiriro+ mwa amene Iyeyo anamutuma.”+ 30 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Ndiye inuyo muchita chizindikiro+ chotani, kuti ife tichione, ndi kukukhulupirirani? Muchita ntchito yotani? 31 Makolo athu anadya mana+ m’chipululu, monga mmene Malemba amanenera kuti, ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+ 32 Pamenepo Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni chakudya chochokera kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba.+ 33 Iye wotsika kuchokera kumwamba, amene amapereka moyo kudziko ndiye chakudya chimene Mulungu amapereka.” 34 Choncho iwo anati: “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenechi nthawi zonse.”+
35 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ine ndine chakudya chopatsa moyo. Aliyense wobwera kwa ine sadzamva njala ngakhale pang’ono, ndipo wokhulupirira mwa ine sadzamva ludzu.+ 36 Koma ndakuuzani kuti, Ngakhale mwandiona, simukukhulupirirabe.+ 37 Chilichonse chimene Atate adzandipatse chidzabwera kwa ine, ndipo wobwera kwa ine sindidzamukana.+ 38 Chifukwa ndinatsika kuchokera kumwamba+ kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.+ 39 Chifuniro cha amene anandituma ine n’chakuti, ndisataye aliyense mwa onse amene iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse+ pa tsiku lomaliza. 40 Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi chakuti, aliyense woona Mwana ndi kukhulupirira mwa iye akhale nawo moyo wosatha,+ ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lomaliza.”+
41 Pamenepo Ayudawo anayamba kung’ung’udza za iye chifukwa ananena kuti: “Ine ndine chakudya chotsika kumwamba.”+ 42 Iwo anayamba kunena kuti:+ “Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe,+ amene bambo ake ndi mayi ake tikuwadziwa? Nanga bwanji pano akunena kuti, ‘Ndinatsika kumwamba’?” 43 Poyankha Yesu anati: “Musang’ung’udze inu. 44 Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine,+ ndipo ine ndidzamuukitsa tsiku lomaliza.+ 45 Zinalembedwa m’Mabuku a Aneneri kuti, ‘Ndipo onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’*+ Aliyense amene wamva kwa Atate ndipo waphunzira amabwera kwa ine.+ 46 Sikuti alipo munthu amene anaonapo Atate ayi,+ kupatulapo yekhayo amene anachokera kwa Mulungu, ameneyu anaona Atate.+ 47 Ndithudi ndikukuuzani, Wokhulupirira ali nawo moyo wosatha.+
48 “Ine ndine chakudya+ chopatsa moyo. 49 Makolo anu anadya mana+ m’chipululu koma anamwalirabe. 50 Ichi ndi chakudya chochokera kumwamba, choti aliyense adyeko kuti asamwalire. 51 Ine ndine chakudya chamoyo chotsika kumwamba. Ngati wina adyako chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo kosatha. Ndipotu chakudya chimene ndidzapereke kuti dzikoli lipeze moyo,+ ndicho mnofu wangawu.”+
52 Pamenepo Ayudawo anayamba kutsutsana okhaokha, kuti: “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipatsa mnofu wake kuti tidye?” 53 Choncho Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mukapanda kudya mnofu+ wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake,+ mulibe moyo+ mwa inu. 54 Wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga ali nawo moyo wosatha, ndipo ndidzamuukitsa+ kwa akufa tsiku lomaliza. 55 Pakuti mnofu wanga ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56 Munthu wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga, iyeyo ndi ine timakhala ogwirizana.+ 57 Monga Atate wamoyo+ anandituma ine, ndipo ine ndili ndi moyo chifukwa cha Atate, momwemonso amene akudya ine, nayenso adzakhala ndi moyo chifukwa cha ine.+ 58 Chimenechi ndiye chakudya chotsika kumwamba. N’chosiyana ndi chakudya chimene makolo anu anadya koma anamwalirabe. Iye wakudya chakudya ichi adzakhala ndi moyo kosatha.”+ 59 Zinthu zimenezi anazinena pamene anali kuphunzitsa m’bwalo losonkhanira ku Kaperenao.
60 Pamenepo ambiri mwa ophunzira ake atamva zimenezi anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsere zimenezi?”+ 61 Koma Yesuyo, pakuti anadziwa payekha kuti ophunzira ake akung’ung’udza pa mawuwo, anafunsa kuti: “Kodi mawuwa mwakhumudwa+ nawo? 62 Nanga zidzakhala bwanji mukadzaona Mwana wa munthu akukwera kupita kumene anali poyamba?+ 63 Mzimu ndi umene umapatsa moyo,+ mnofu n’ngopanda phindu. Mawu amene ndakuuzaniwa ndiwo mzimu+ ndiponso ndiwo moyo.+ 64 Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti kuchokera pa chiyambi, Yesu anadziwa amene sanali kukhulupirira komanso amene adzamupereka.+ 65 Choncho anapitiriza kunena kuti: “N’chifukwa chake ndinakuuzani kuti, Munthu sangabwere kwa ine popanda Atate kumulola.”+
66 Pa chifukwa chimenechi ophunzira ake ambiri anamusiya ndi kubwerera ku zinthu zakumbuyo,+ ndipo sanayendenso naye.+ 67 Tsopano Yesu anafunsa ophunzira ake 12 aja kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” 68 Simoni Petulo+ anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani?+ Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.+ 69 Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.”+ 70 Pamenepo Yesu anati: “Ine ndinakusankhani inu 12,+ si choncho kodi? Komatu mmodzi wa inu ndi wonenera anzake zoipa.”+ 71 Kwenikweni iye anali kunena za Yudasi mwana wa Simoni Isikariyoti, pakuti ameneyu anali kudzamupereka,+ ngakhale anali mmodzi wa ophunzira 12 amenewo.
7 Zimenezi zitatha, Yesu anapitiriza kuyendayenda mu Galileya. Iye sanafune kumayendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anali kufunitsitsa kumupha.+ 2 Komabe chikondwerero cha Ayuda, chikondwerero cha misasa+ chinali pafupi. 3 Chotero abale ake+ anamupempha kuti: “Mupite ku Yudeya kuti ophunzira anunso akaone zimene mukuchita. 4 Pakuti palibe amene amachita kanthu mseri koma n’kumafuna kudziwika ndi anthu. Ngati inu mumachita zimenezi, mudzionetsere poyera kudzikoli.” 5 Abale akewo+ sanali kumukhulupirira.+ 6 Chotero Yesu anati: “Nthawi yanga yoyenera sinakwanebe,+ koma kwa inu, iliyonse ndi nthawi yanu yoyenera. 7 Dziko lilibe chifukwa chodana ndi inu, koma limadana ndi ine, chifukwa ndimachitira umboni kuti dzikoli ntchito zake ndi zoipa.+ 8 Inuyo nyamukani mupite ku chikondwereroko. Ine sindipitako panopa, chifukwa nthawi yanga yoyenera+ sinafike.”+ 9 Atawauza zimenezi, iye anatsalira mu Galileya.
10 Koma abale akewo atanyamuka kupita ku chikondwereroko, iyenso ananyamuka payekha. Sanapite moonekera koma mwamseri.+ 11 Chotero Ayuda anayamba kumufunafuna+ ku chikondwereroko. Iwo anali kunena kuti: “Kodi munthu ujayu ali kuti?” 12 Ndipo panali manong’onong’o ambiri onena za iye m’khamu lonse la anthulo.+ Ena anali kunena kuti: “Amene uja ndi munthu wabwino.” Ndipo ena anali kunena kuti: “Ayi si munthu wabwino amene uja, iye akusocheretsa anthu ambiri.” 13 Koma panalibe amene anali kulankhula poyera za iye chifukwa choopa Ayuda.+
14 Tsopano chikondwererocho chitafika pakatikati, Yesu analowa m’kachisi ndipo anayamba kuphunzitsa.+ 15 Pamenepo Ayudawo anayamba kudabwa ndi kufunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu zolembazi anazidziwa bwanji,+ popeza sanapite kusukulu?”+ 16 Yesu anawayankha kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.+ 17 Ngati munthu akufuna kuchita chifuniro cha amene ananditumayo, adzadziwa za chiphunzitsochi ngati chili chochokera kwa Mulungu,+ kapena ngati ndimalankhula za m’maganizo mwanga. 18 Wolankhula za m’maganizo mwake amadzifunira yekha ulemerero.+ Koma wofunira ulemerero iye amene anamutuma, ameneyu ali woona, ndipo mwa iye mulibe kusalungama. 19 Mose anakupatsani Chilamulo,+ si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale mmodzi wa inu amene amamvera Chilamulocho. Nanga n’chifukwa chiyani inu mukufuna kundipha?”+ 20 Khamu la anthulo linayankha kuti: “Uli ndi chiwanda iwe.+ Akufuna kukupha ndani?” 21 Poyankha Yesu anati: “Ndangochita chinthu chimodzi chabe,+ ndipo nonsenu mukudabwa. 22 Pa chifukwa chimenechi Mose anakupatsani mdulidwe.+ Sikuti mdulidwewo ndi wochokera kwa Mose ayi, koma ndi wochokera kwa makolo akale,+ ndipo mumachita mdulidwe tsiku la sabata. 23 Ngati munthu amadulidwa tsiku la sabata posafuna kuphwanya chilamulo cha Mose, kodi mukundipsera mtima ine chifukwa ndinachiritsa munthu tsiku la sabata?+ 24 Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”+
25 Pamenepo anthu ena okhala mu Yerusalemu anayamba kunena kuti: “Si ameneyu kodi akufuna kumupha uja?+ 26 Koma taonani! Si uyu akulankhula poyera apa,+ ndipo palibe akunenapo kanthu kwa iye. Olamulirawo sakutsimikiza ngati iyeyo alidi Khristu eti?+ 27 Koma ife tikudziwa kumene munthu ameneyu akuchokera.+ Komano Khristuyo akadzabwera, palibe amene adzadziwe kumene wachokera.”+ 28 Chotero pamene anali kuphunzitsa m’kachisimo Yesu anafuula kuti: “Inu mukundidziwa ine komanso mukudziwa kumene ndikuchokera.+ Ndipo ine sindinabwere mwa kufuna kwanga,+ alipo ndithu amene anandituma,+ koma inu simukumudziwa.+ 29 Ine ndikumudziwa,+ chifukwa ndine nthumwi. Iyeyu anandituma ine.”+ 30 Pamenepo anayamba kufufuza njira yomugwirira,+ koma palibe amene anamugwira chifukwa nthawi yake+ inali isanafike. 31 Komabe ochuluka m’khamu la anthulo anakhulupirira mwa iye+ ndipo anayamba kunena kuti: “Akadzafika Khristu, kodi adzachita zizindikiro zochuluka+ kuposa zimene munthu uyu wachita?”
32 Afarisi anamva khamu la anthulo likunong’onezana motero za iye, ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma alonda kuti akamugwire.+ 33 Pamenepo Yesu anati: “Ndikhala nanube kanthawi pang’ono ndisanapite kwa iye amene anandituma.+ 34 Mudzandifunafuna,+ koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapiteko inu simudzatha kukafikako.”+ 35 Chotero Ayudawo anayamba kufunsana kuti: “Ameneyu akufuna kupita kuti, kumene ife sitingathe kukam’peza? Kapena akufuna kupita kwa Ayuda omwazikana+ mwa Agiriki ndi kukaphunzitsa Agirikiwo? 36 Kodi akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza, ndipo kumene ine ndidzapite inu simudzatha kukafikako’?”
37 Tsopano pa tsiku lomaliza, tsiku lalikulu la chikondwererocho,+ Yesu anaimirira ndi kufuula kuti: “Ngati wina akumva ludzu,+ abwere kwa ine adzamwe madzi. 38 Wokhulupirira mwa ine,+ ‘Mkati mwake mwenimwenimo mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo,’ monga mmene Malemba amanenera.”+ 39 Pamenepa anali kunena za mzimu umene onse okhulupirira mwa iye anali pafupi kulandira. Pakuti pa nthawiyi n’kuti asanaulandire,+ chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.+ 40 Choncho ena m’khamulo, amene anamva mawu amenewa, anayamba kunena kuti: “Ameneyu ndi Mneneri ndithu.”+ 41 Ena anali kunena kuti: “Khristu uja ndi ameneyu.”+ Koma ena anati: “Iyayi, kodi Khristu+ angachokere mu Galileya?+ 42 Kodi Malemba sanena kuti Khristu adzatuluka mwa ana a Davide,+ komanso mu Betelehemu+ mudzi umene Davide anali kukhala?”+ 43 Choncho khamu la anthulo linagawanika pa nkhani ya iye.+ 44 Ena a iwo anali kufunitsitsa kumugwira, koma palibe ngakhale mmodzi amene anamukhudza.
45 Tsopano alonda aja anabwerera kwa ansembe aakulu ndi Afarisi. Ndiyeno iwowa anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simunabwere naye?” 46 Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.”+ 47 Pamenepo Afarisiwo anati: “Kodi inunso mwasocheretsedwa? 48 Palibe ndi mmodzi yemwe mwa olamulira kapena Afarisi amene wakhulupirira mwa iye, alipo ngati?+ 49 Koma khamu lonseli la anthu osadziwa Chilamulo ndi lotembereredwa.”+ 50 Nikodemo, amene m’mbuyomo anabwera kwa iye, komanso anali mmodzi wa iwo, anawauza kuti: 51 “Chilamulo chathu sichiweruza munthu asanafotokoze maganizo ake choyamba+ ndi kudziwa zochita zake, chimatero ngati?” 52 Poyankha iwo anati: “Kodi iwenso ndiwe wochokera ku Galileya eti? Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati m’Galileya mudzatuluka mneneri.”*+
* Mipukutu ya Codex Sinaiticus, Codex Vaticanus ndi Sinaitic Syriac, inachotsa vesi 53 mpaka chaputala 8, vesi 11. (M’mabuku ambiri Achigiriki mawu a mavesi amenewa amasiyanasiyana.) Ndimezi zili ndi mawu akuti:
53 Zitatero aliyense ananyamuka n’kupita kwawo.
8 Kenako Yesu anapita kuphiri la Maolivi. 2 M’mawa kwambiri, anafikanso kukachisi ndipo anthu onse anayamba kubwera kwa iye. Choncho iye anakhala pansi ndi kuyamba kuwaphunzitsa. 3 Tsopano alembi ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Ndipo atamuimika pakati pawo, 4 anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa akuchita chigololo. 5 M’Chilamulo, Mose analamula kuti akazi oterewa tiziwaponya miyala. Nanga inu mukutipo bwanji?” 6 Iwo kwenikweni anali kunena zimenezi pofuna kungomuyesa, kuti amupeze chifukwa chomuimbira mlandu. Koma Yesu anawerama ndi kuyamba kulemba pansi ndi chala chake. 7 Atalimbikira kumufunsa, iye anaweramuka ndi kuwauza kuti: “Munthu amene ali wopanda tchimo pakati panu, ayambe iyeyo kumuponya mwala mkaziyu.” 8 Kenako anaweramanso ndi kupitiriza kulemba pansi. 9 Koma iwo atamva zimenezi, anayamba kuchoka mmodzimmodzi. Oyamba kuchoka anali akulu, mpaka Yesu anamusiya yekha ndi mkazi amene anali pakati pawo uja. 10 Tsopano Yesu ataweramuka, anafunsa mkaziyo kuti: “Mayi iwe, anthu aja ali kuti? Kodi palibe amene waona kuti ndiwe woyenera kulangidwa?” 11 Mkaziyo anati: “Palibe bambo.” Ndiyeno Yesu anati: “Inenso sindikuona kuti ndiwe woyenera kulangidwa. Pita, kuyambira lero usakachitenso tchimo.”
12 Pamenepo Yesu analankhula nawonso kuti: “Ine ndine kuwala+ kwa dziko. Wonditsatira ine sadzayenda mumdima,+ koma adzakhala nako kuwala kwa moyo.” 13 Chotero Afarisi anauza Yesu kuti: “Iwe umadzichitira wekha umboni koma umboni wakowo si woona ayi.” 14 Poyankha Yesu anati: “Ngakhale kuti ndimadzichitira ndekha umboni,+ umboni wanga ndi woona, chifukwa ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita.+ Koma inu simukudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. 15 Inu mumaweruza mwa kungoona maonekedwe a munthu.+ Inetu sindiweruza munthu aliyense.+ 16 Koma ndikati ndiweruze, chiweruzo changa chimakhala cholungama, chifukwa sindiweruza ndekha, pakuti Atate amene anandituma ali ndi ine.+ 17 Ndiponso m’Chilamulo chanu chomwechi analembamo kuti, ‘Umboni wa anthu awiri ndi woona.’+ 18 Ineyo pandekha ndimadzichitira umboni, ndipo Atate amene anandituma amandichitiranso umboni.”+ 19 Pamenepo iwo anati: “Atate wako ali kuti?” Yesu anayankha kuti: “Inu simukundidziwa ine kapena Atate wanga.+ Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga.”+ 20 Ananena mawu amenewa ali m’malo a zopereka+ pamene anali kuphunzitsa m’kachisi. Koma palibe amene anamugwira,+ chifukwa nthawi yake+ inali isanafikebe.
21 Choncho iye anawauzanso kuti: “Ine ndikuchoka ndipo mudzandifunafuna,+ koma mudzafabe m’tchimo lanu.+ Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako.” 22 Pamenepo Ayudawo anayamba kunena kuti: “Kodi akufuna kudzipha? Nanga n’chifukwa chiyani akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako?’”+ 23 Iye anawauza kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano, ine ndine wochokera kumwamba.+ Inu ndinu ochokera m’dziko lino,+ ine si wochokera m’dziko lino.+ 24 N’chifukwa chake ndakuuzani kuti, Inu mudzafa m’machimo anu.+ Pakuti ngati simukhulupirira kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja, mudzafa m’machimo anu.”+ 25 Choncho iwo anayamba kunena kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?” Yesu anati: “N’chifukwa chiyani ndikudzivuta kulankhula nanu? 26 Ndili ndi zambiri zoti ndinene zokhudza inu ndi kuperekerapo chiweruzo. Ndipotu amene anandituma ine amanena zoona. Zimene ndinamva kwa iye, zomwezo ndikuzilankhula m’dzikoli.”+ 27 Iwo sanazindikire kuti anali kunena za Atatewo. 28 Pamenepo Yesu anati: “Mukadzamukweza+ Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja,+ ndi kutinso sindichita kanthu mongoganiza ndekha.+ Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.+ 29 Ndipo amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha, chifukwa ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.”+ 30 Pamene anali kulankhula zimenezi, ambiri anakhulupirira mwa iye.+
31 Chotero Yesu anapitiriza kuuza Ayuda amene anamukhulupirirawo kuti: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse,+ ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. 32 Mudzadziwa choonadi,+ ndipo choonadi chidzakumasulani.”+ 33 Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu ndife ana a Abulahamu+ ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu.+ Tsopano iwe ukunena bwanji kuti, ‘Mudzamasulidwa’?” 34 Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimo.+ 35 Komanso, kapolo sakhala m’banjamo kwamuyaya, mwana ndiye amakhalamo kwamuyaya.+ 36 Choncho ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.+ 37 Ndikudziwa kuti ndinu ana a Abulahamu, koma mukufuna kundipha,+ chifukwa mawu anga sakukhazikika mwa inu.+ 38 Zimene ndinaziona kwa Atate wanga+ ndi zimene ndimalankhula.+ Chotero inunso mumachita zimene mwamva kwa atate wanu.” 39 Poyankha iwo anati: “Atate wathu ndi Abulahamu.”+ Yesu anawauza kuti: “Ngati ndinu ana a Abulahamu,+ chitani ntchito za Abulahamu. 40 Koma tsopano mukufuna kundipha ine, munthu amene ndakuuzani choonadi chimene ndinachimva kwa Mulungu.+ Abulahamu sanachite zimenezi.+ 41 Inu mumachita ntchito za atate wanu.” Iwo anati: “Ife sitinabadwe m’chigololo,* tili ndi Atate mmodzi,+ ndiye Mulungu.”
42 Pamenepo Yesu anati: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda,+ pakuti ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano.+ Sindinabwere mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.+ 43 N’chifukwa chiyani mukulephera kuzindikira zimene ine ndikunena? N’chifukwa chakuti simukufuna kumvetsera mawu anga.+ 44 Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi,+ ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu.+ Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake,+ ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.+ 45 Koma popeza ine ndimanena zoona, simundikhulupirira.+ 46 Ndani wa inu amene angandipeze ndi mlandu wa tchimo? Ndipo ngati ndimanena zoona, n’chifukwa chiyani simundikhulupirira?+ 47 Wochokera kwa Mulungu amamvetsera mawu a Mulungu.+ Ndiye chifukwa chake inu simumvetsera, chifukwa sindinu ochokera kwa Mulungu.”+
48 Poyankha Ayudawo anati: “Kodi tikamanena kuti, Ndiwe Msamariya+ ndipo uli ndi chiwanda,+ tikulakwitsa ngati?” 49 Yesu anayankha kuti: “Ndilibe chiwanda ine, ndimalemekeza Atate wanga,+ koma inu mukundinyoza. 50 Komatu ine sindikudzifunira ndekha ulemerero.+ Alipo Wina amene akuufuna ndipo iye ndi woweruza.+ 51 Ndithudi ndikukuuzani, ngati munthu akusunga mawu anga, sadzaona imfa.”+ 52 Ayudawo anati: “Tsopano tadziwa ndithu kuti uli ndi chiwanda.+ Abulahamu anamwalira,+ ndiponso aneneri.+ Koma iwe ukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga sadzalawa+ imfa.’ 53 Kodi iweyo ndiwe wamkulu+ kuposa atate wathu Abulahamu amene anamwalira? Aneneri nawonso anamwalira.+ Ndiye iweyo ukudziyesa ndani?” 54 Yesu anayankha kuti: “Ngati ndikudzilemekeza ndekha, ndiye kuti ulemerero wanga ndi wopanda pake. Atate wanga ndi amene amandilemekeza,+ amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, 55 chikhalirecho simukumudziwa.+ Koma ine ndikumudziwa.+ Ngati ndinganene kuti sindikumudziwa ndingakhale wabodza, kufanana ndi inuyo. Koma ndikumudziwa ndithu ndipo ndikusunga mawu ake.+ 56 Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezera kuona tsiku langa,+ ndipo analiona moti anakondwera.”+ 57 Pamenepo Ayudawo anati: “Zaka 50 zakubadwa sunakwanitse n’komwe, ndiye ukuti unamuona Abulahamu?” 58 Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko, ine n’kuti ndilipo kale.”+ 59 Pamenepo anatola miyala kuti amugende nayo,+ koma Yesu anabisala ndi kutuluka m’kachisimo.
9 Tsopano pamene anali kuyenda anaona munthu amene anabadwa wakhungu. 2 Ophunzira ake anamufunsa kuti: “Rabi,+ anachimwa ndani+ kuti munthu uyu abadwe wakhungu chonchi? Ndi iyeyu kapena makolo ake?”+ 3 Yesu anayankha kuti: “Munthuyu kapena makolo ake, onsewa palibe amene anachimwa. Izi zinachitika kuti ntchito za Mulungu zionekere kudzera mwa iye.+ 4 Tiyenera kugwira ntchito za iye amene anandituma ine kudakali masana.+ Usiku+ ukubwera pamene munthu sangathe kugwira ntchito. 5 Pamene ine ndili m’dziko, ndine kuwala kwa dzikoli.”+ 6 Atanena zimenezi, analavulira malovu pansi ndi kukanda thope ndi malovuwo. Atatero anapaka thopelo m’maso mwa munthuyo.+ 7 Kenako anamuuza kuti: “Pita ukasambe+ m’dziwe la Siloamu”+ (dzina limene kumasulira kwake ndi ‘Otumidwa’). Choncho anapita kukasamba,+ ndipo anabwerako akuona.+
8 Tsopano anthu okhala naye pafupi ndi anthu ena amene m’mbuyomo anali kumuona akupemphapempha anayamba kunena kuti: “Si uyu kodi amene anali kukhala pansi n’kumapemphapempha uja?”+ 9 Ena anati: “Ndi yemweyu.” Enanso anati: “Iyayi, wangofanana naye.” Mwiniwakeyo anati: “Ndine amene.” 10 Pamenepo anayamba kumufunsa kuti: “Nanga maso akowa atseguka bwanji?”+ 11 Iye anayankha kuti: “Munthu wina dzina lake Yesu anakanda thope ndi kupaka m’maso mwangamu, ndiyeno anandiuza kuti, ‘Pita ku Siloamu+ ukasambe.’ Ndinapitadi kukasamba ndipo ndayamba kuona.” 12 Pamenepo anthuwo anamufunsa kuti: “Ali kuti munthu ameneyo?” Iye anati: “Sindikudziwa.”
13 Iwo anatenga munthu amene anali wakhunguyo ndi kupita naye kwa Afarisi. 14 Tsiku limene Yesu anakanda matope ndi kutsegula maso a munthuyo,+ linali la Sabata.+ 15 Pamenepo Afarisi nawonso anayamba kufunsa munthu uja mmene anayambira kuona.+ Iye anawafotokozera kuti: “Iye anapaka thope m’maso mwanga, ndiyeno ndinapita kukasamba, basi kenako ndayamba kuona.” 16 Ena mwa Afarisiwo anayamba kunena kuti: “Munthu ameneyu si wochokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.”+ Ena anayamba kunena kuti: “Koma munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro+ zoterezi?” Choncho panakhala kugawanika+ pakati pawo. 17 Ndiyeno Afarisiwo anafunsanso munthu amene anali wakhungu uja kuti: “Nanga iwe ukuti bwanji za munthu ameneyu, popeza kuti wakutsegula maso?” Munthuyo anati: “Ndi mneneri.”+
18 Komabe atsogoleri achipembedzo achiyudawo sanakhulupirire zakuti munthuyu analidi wakhungu ndipo wayamba kuona, mpaka anaitanitsa makolo ake. 19 Makolowo anawafunsa kuti: “Kodi uyu ndi mwana wanu amene mukuti anabadwa wakhungu? Nanga zatheka bwanji kuti tsopano aziona?” 20 Pamenepo makolo akewo anayankha kuti: “Tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu ndi kuti anabadwa wakhungu. 21 Koma za mmene wayambira kuona tsopano, ndi amene wamutsegula maso, zimenezo sitikudziwapo kanthu ayi. Mufunseni mwiniwakeyu. Ndi wamkulu, afotokoze yekha.” 22 Makolo akewo ananena zimenezi chifukwa anali kuopa+ atsogoleri achipembedzo achiyuda. Pakuti iwo anali atagwirizana kale kuti, ngati wina angavomereze kuti Yesu alidi Khristu, adzamuchotsa musunagoge.+ 23 N’chifukwa chake makolo akewo ananena kuti: “Ndi wamkulu. Mufunseni mwiniwakeyu.”
24 Choncho iwo anaitananso munthu anali wakhungu uja kachiwiri ndi kumuuza kuti: “Lemekeza Mulungu,+ ife tikudziwa kuti munthu ameneyu ndi wochimwa.” 25 Iye anayankha kuti: “Zakuti iye ndi wochimwa, ine sindikudziwa. Chimodzi chokha chimene ine ndikudziwa n’chakuti, poyamba ndinali wakhungu, koma tsopano ndikuona.” 26 Pamenepo iwo anati: “Anakuchita chiyani? Watsegula bwanji maso ako?” 27 Iye anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simunamvetsere. Nanga n’chifukwa chiyani mukufuna kumvanso? Kapena inunso mukufuna kukhala ophunzira ake?” 28 Atanena zimenezi, iwo anamulalatira kuti: “Iweyo ndiye wophunzira wa munthu amene uja, ifetu ndife ophunzira a Mose. 29 Tikudziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose,+ koma za munthu uyu, sitikudziwa kuti iye akuchokera kuti.”+ 30 Poyankha munthuyo anati: “Izi n’zodabwitsa ndithu,+ simukudziwa kumene wachokera, chikhalirecho wanditsegula maso. 31 Tikudziwa kuti Mulungu samvetsera ochimwa,+ koma ngati munthu ali woopa Mulungu ndipo amachita chifuniro chake, ameneyo amamumvetsera.+ 32 Sizinamveke n’kale lonse kuti wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu. 33 Munthu uyu akanapanda kuchokera kwa Mulungu,+ sakanatha kuchita kanthu.” 34 Poyankha iwo anati: “Wobadwira mu uchimo wokhawokha iwe,+ ukufuna kuphunzitsa ife kodi?” Pamenepo anamuchotsa musunagoge!+
35 Yesu anamva kuti munthu uja amuchotsa musunagoge. Ndipo atakumana naye anamufunsa kuti: “Kodi ukukhulupirira mwa Mwana+ wa munthu?” 36 Munthuyo anayankha kuti: “Kodi mwana wa munthuyo ndani ndimudziwe bambo, kuti ndikhulupirire mwa iye?” 37 Yesu anamuuza kuti: “Wamuona kale, ndi amene akulankhula nawe panopa.”+ 38 Pamenepo iye ananena kuti: “Ndakhulupirira mwa iye Ambuye.” Ndipo anamugwadira.+ 39 Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Ndinabwera m’dziko lino kudzapereka chiweruzo ichi:+ Osaona ayambe kuona,+ ndipo oona akhale akhungu.”+ 40 Afarisi amene anali naye anamva zimenezi, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi ifenso tingakhale akhungu?”+ 41 Yesu anati: “Mukanakhala akhungu, simukanakhala ndi tchimo. Koma popeza mukunena kuti, ‘Tikuona.’+ Tchimo+ lanu likhalabe chikhalire.”
10 “Ndithudi ndikukuuzani, Wolowa m’khola la nkhosa mochita kukwera pamalo ena osati kudzera pakhomo,+ ameneyo ndi wakuba ndiponso wofunkha.+ 2 Koma wolowera pakhomo,+ ameneyo ndiye m’busa+ wa nkhosazo.+ 3 Mlonda wa pakhomo+ amamutsegulira ameneyu, ndipo nkhosa+ zimamvera mawu ake. Nkhosa zakezo amazitchula mayina ndi kuzitsogolera kutuluka nazo. 4 Akatulutsa zake zonse kunja, amazitsogolera, ndipo nkhosazo zimamutsatira,+ chifukwa zimadziwa mawu ake.+ 5 Mlendo sizidzamutsatira ayi koma zidzamuthawa,+ chifukwa sizidziwa mawu a alendo.”+ 6 Yesu ananena fanizoli kwa iwo, koma iwo sanadziwe tanthauzo la zinthu zimene anali kuwauzazo.+
7 Choncho Yesu anawauzanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Ine ndine khomo+ la nkhosa. 8 Onse amene abwera m’malo mwa ine ndi akuba ndiponso ofunkha,+ ndipo nkhosa sizinawamvere.+ 9 Ine ndine khomo.+ Aliyense wolowa kudzera mwa ine adzapulumuka, ndipo azidzalowa ndi kutuluka, kukapeza msipu.+ 10 Wakuba+ sabwera ndi cholinga china ayi, koma kudzaba, kudzapha ndi kudzawononga.+ Koma ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka. 11 Ine ndine m’busa wabwino.+ M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.+ 12 Munthu waganyu,+ amene si m’busa ndipo nkhosazo si zake, akaona mmbulu ukubwera amasiya nkhosazo ndi kuthawa, pamenepo mmbuluwo umazigwira ndi kuzibalalitsa,+ 13 chifukwa iye ndi waganyu+ chabe, ndipo sasamala za nkhosazo.+ 14 Ine ndine m’busa wabwino, nkhosa zanga ndimazidziwa,+ izonso zimandidziwa,+ 15 monga mmene zilili kuti Atate amandidziwa, inenso ndimawadziwa Atate.+ Chotero, ndipereka moyo wanga chifukwa cha nkhosazo.+
16 “Ndili ndi nkhosa zina+ zimene sizili za khola ili,+ zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga,+ ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.+ 17 Chimene Atate amandikondera n’chakuti,+ ndikupereka moyo wanga+ kuti ndikaulandirenso. 18 Palibe munthu amene akuuchotsa kwa ine, koma ndikuupereka mwa kufuna kwanga. Ndili ndi mphamvu zoupereka, ndiponso ndili ndi mphamvu zoulandiranso.+ Atate wanga ndi amene anandilamula+ kuchita zimenezi.”
19 Apanso panakhala kugawanika+ maganizo pakati pa Ayuda chifukwa cha mawu amenewa. 20 Ambiri a iwo anali kunena kuti: “Ameneyu ali ndi chiwanda+ ndipo ndi wamisala. N’chifukwa chiyani mukumumvetsera?” 21 Ena anali kunena kuti: “Amenewa si mawu a munthu wogwidwa ndi chiwanda ayi. Kodi chiwanda chingatsegule maso a anthu akhungu?”
22 Pa nthawiyo mu Yerusalemu munachitika chikondwerero cha kupereka kachisi kwa Mulungu. Inali nyengo ya chisanu, 23 ndipo Yesu anali kuyenda m’kachisimo, m’khonde la zipilala la Solomo.+ 24 Choncho Ayuda anamuzungulira ndi kuyamba kumuuza kuti: “Utivutitsa maganizo mpaka liti? Ngati ndiwedi Khristu,+ tiuze mosapita m’mbali.”+ 25 Yesu anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simukukhulupirira. Ntchito zimene ine ndikuchita m’dzina la Atate wanga, zikundichitira umboni.+ 26 Koma inu simukukhulupirira, chifukwa si inu nkhosa zanga.+ 27 Nkhosa+ zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziwa, ndipo izo zimanditsatira.+ 28 Ndidzazipatsa moyo wosatha,+ moti sizidzawonongeka,+ komanso palibe amene adzazitsomphole m’dzanja langa.+ 29 Chimene Atate+ wanga wandipatsa n’chofunika kuposa zinthu zonse,+ ndipo palibe amene angazitsomphole m’dzanja la Atate.+ 30 Ine ndi Atate ndife amodzi.”+
31 Apanso Ayudawo anatola miyala kuti amugende.+ 32 Yesu anawauza kuti: “Ndakuonetsani ntchito zambiri zabwino zochokera kwa Atate. Tsopano mukundiponya miyala chifukwa cha ntchito iti mwa zimenezi?” 33 Ayudawo anamuyankha kuti: “Sitikukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ayi, koma chifukwa chonyoza Mulungu.+ Iwe ndiwe munthu wamba koma ukudziyesa mulungu.”+ 34 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo chanu sanalembemo+ kuti, ‘Ine ndinati: “Inu ndinu milungu”’?+ 35 Ngati anthu amene anatsutsidwa ndi mawu a Mulungu anawatcha ‘milungu,’+ ndipo Malemba satha mphamvu,+ 36 nanga kodi inu mukundiuza ine woyeretsedwa ndi Atate ndi kutumizidwa m’dziko kuti, ‘Ukunyoza Mulungu,’ chifukwa ndanena kuti, Ndine Mwana wa Mulungu?+ 37 Ngati sindikuchita ntchito+ za Atate wanga, musandikhulupirire. 38 Koma ngati ndikuzichita, ngakhale simukundikhulupirira, khulupirirani ntchitozo,+ kuti mudziwe ndi kupitirizabe kudziwa kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana.”+ 39 Pamenepo anayesanso kumugwira,+ koma anawazemba.+
40 Chotero anawolokanso Yorodano ndi kupita kumene Yohane anali kubatizira+ poyamba, ndipo anakhala kumeneko. 41 Anthu ambiri anabwera kwa iye, ndi kuyamba kunena kuti: “Yohane sanachite chizindikiro chilichonse, koma zonse zimene Yohane ananena zokhudza munthu uyu zinali zoona.”+ 42 Choncho anthu ambiri kumeneko anamukhulupirira.+
11 Tsopano panali munthu wina amene anali kudwala, dzina lake Lazaro. Anali wa m’mudzi wa Betaniya, kwawo kwa Mariya ndi m’bale wake Marita.+ 2 Mariyayu ndi yemwe uja amene anathira Ambuye mafuta onunkhira+ ndi kupukuta mapazi awo ndi tsitsi lake.+ Lazaro amene anali kudwalayu anali mlongo wake. 3 Choncho alongo akewo anatumiza uthenga kwa Yesu, kuti: “Ambuye! amene mumamukonda+ uja akudwala.” 4 Koma Yesu atamva zimenezi ananena kuti: “Kudwala kumeneku si kwa imfa chabe, koma n’kopatsa Mulungu ulemerero,+ kuti mwa kudwalako, Mwana wa Mulungu alemekezeke.”
5 Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro. 6 Koma atamva kuti Lazaro akudwala, anakhalabe masiku awiri kumalo kumene iye anali. 7 Pambuyo pake anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” 8 Ophunzirawo anati: “Rabi,+ posachedwapa Ayudeya anafuna kukuponyani miyala,+ ndiye mukufuna kupitanso komweko kodi?” 9 Yesu anayankha kuti: “Kodi usana suli ndi maola 12? Munthu akayenda masana+ palibe chimamupunthwitsa, chifukwa amaona kuwala kwa dzikoli. 10 Koma munthu akayenda usiku,+ amapunthwa pa chinachake chifukwa mwa iye mulibe kuwala.”
11 Atanena zimenezi, kenako anauza ophunzira akewo kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.”+ 12 Pamenepo ophunzirawo anati: “Ambuye, ngati iye akupumula, apeza bwino.” 13 Apa Yesu anali kunena za imfa yake. Koma iwo anaganiza kuti anali kunena za kugona tulo teniteni. 14 Choncho, Yesu tsopano anawauza momveka bwino kuti: “Lazaro wamwalira,+ 15 ndipo ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti sindinali kumeneko, kuti inu mukhulupirire. Tsopano tiyeni tipite kwa iye.” 16 Choncho Tomasi, wotchedwa Didimo, anauza ophunzira anzakewo kuti: “Ifenso tiyeni tipite, kuti tikafere naye limodzi.”+
17 Tsopano Yesu atafika kumeneko, anapeza kuti Lazaro wakhala kale m’manda achikumbutso masiku anayi.+ 18 Mzinda wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wa makilomita pafupifupi atatu. 19 Tsopano Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza+ chifukwa cha imfa ya mlongo wawo. 20 Choncho Marita atamva kuti Yesu akubwera, anakamuchingamira, koma Mariya+ anakhalabe kunyumba. 21 Marita anauza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.+ 22 Komabe, ngakhale tsopano ndikudziwa kuti zilizonse zimene mungapemphe Mulungu,+ Mulungu adzakupatsani zonsezo.” 23 Yesu anamuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.”+ 24 Marita anati: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa+ m’tsiku lomaliza.” 25 Pamenepo Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.+ Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.+ 26 Ndipo aliyense amene ali moyo ndi kukhulupirira mwa ine sadzafa ayi.+ Kodi ukukhulupirira zimenezi?” 27 Iye anayankha kuti: “Inde, Ambuye. Ndimakhulupirira kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, Amene dziko linali kuyembekezera kubwera kwake.”+ 28 Pamene ananena zimenezi, anapita kukaitana m’bale wake Mariya ndi kumuuza mseri kuti: “Mphunzitsi+ ali pano ndipo akukuitana.” 29 Mariya atamva zimenezo, ananyamuka mwamsanga kupita kumene iye anali.
30 Pa nthawiyi n’kuti Yesu asanalowe kwenikweni m’mudzimo. Anali adakali kumalo kumene Marita anakumana naye. 31 Choncho Ayuda amene anali naye pamodzi m’nyumbamo,+ amene anali kumutonthoza, ataona Mariya akunyamuka mofulumira ndi kutuluka kunja, anamutsatira. Anali kuganiza kuti akupita kumanda achikumbutso+ kukalira kumeneko. 32 Tsopano Mariya atafika kumene kunali Yesu kuja ndi kumuona, anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi pafupi ndi mapazi a Yesu. Kenako anamuuza kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.”+ 33 Ndipo Yesu atamuona akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye pamodzi akuliranso, anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.+ 34 Kenako anafunsa kuti: “Mwamuika kuti?” Iwo anati: “Ambuye tiyeni mukaone.” 35 Yesu anagwetsa misozi.+ 36 Pamenepo Ayudawo anayamba kunena kuti: “Taonani, anali kumukondadi kwambiri!”+ 37 Koma ena mwa iwo anati: “Kodi iyeyu, amene anatsegula maso+ a munthu wakhungu uja, sakanatha kuchitapo kanthu kuti mnzakeyu asamwalire?”
38 Koma Yesu atadzumanso movutika mtima, anafika kumanda achikumbutsowo.+ Kwenikweni linali phanga, ndipo analitseka ndi chimwala.+ 39 Yesu anati: “Chotsani chimwalachi.”+ Marita, mlongo wa womwalirayo anauza Yesu kuti: “Ambuye, pano ayenera kuti wayamba kununkha, pakuti lero ndi tsiku lachinayi chimuikireni m’manda.” 40 Yesu anati: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupirira udzaona ulemerero wa Mulungu?”+ 41 Pamenepo anachotsa chimwalacho. Tsopano Yesu anakweza maso ake kumwamba+ ndi kunena kuti: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva.+ 42 Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikunena izi chifukwa cha khamu la anthu+ aimirira panowa, kuti akhulupirire kuti inu munandituma ine.”+ 43 Atanena zimenezi, anafuula mokweza mawu kuti: “Lazaro, tuluka!”+ 44 Amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro,+ nkhope yakenso inali yomanga ndi nsalu. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “M’masuleni ndi kumuleka apite.”
45 Pamenepo Ayuda ambiri amene anabwera kwa Mariya ndi kuona zimene Yesu anachitazo anakhulupirira mwa iye.+ 46 Ena a iwo anapita kwa Afarisi ndi kukawauza zimene Yesu wachita.+ 47 Zitatero ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa Khoti Lalikulu la Ayuda*+ ndi kunena kuti: “Kodi tichite chiyani pamenepa, chifukwa munthu uyu akuchita zizindikiro zochuluka?+ 48 Ngati timulekerera, onse adzakhulupirira mwa iye,+ ndipo Aroma+ adzabwera kudzatenga malo athu+ ndi mtundu wathu.” 49 Koma mmodzi wa iwo, Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho,+ anati: “Palibe chimene mukudziwa inu, 50 ndipo simukuona kuti n’kopindulitsa kwa inu kuti munthu mmodzi afere+ anthu onse, kuti mtundu wonse usawonongeke.”+ 51 Zimene ananenazi, kwenikweni sanaziganize mwa iye yekha, koma chifukwa anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, ananenera kuti Yesu adzafera mtunduwo. 52 Ndipo osati kufera mtundu chabe, komanso kuti asonkhanitse pamodzi+ ana a Mulungu obalalika.+ 53 Choncho kuyambira tsiku limenelo anapangana kuti amuphe.+
54 Pa chifukwa chimenechi, Yesu sanalinso kuyendayenda moonekera+ kwa Ayuda.+ Koma anachoka kumeneko ndi kupita kudera lina lapafupi ndi chipululu, mumzinda wotchedwa Efuraimu.+ Ndipo anakhala kumeneko pamodzi ndi ophunzira ake. 55 Tsopano pasika+ wa Ayuda anali pafupi, ndipo anthu ochuluka anachoka m’midzi ndi kupita ku Yerusalemu pasikayo asanafike, kuti akachite mwambo wa kudziyeretsa.+ 56 Choncho iwo anayamba kufunafuna Yesu ndipo anali kuima pamalo amodzi m’kachisimo ndi kuyamba kukambirana kuti: “Mukuganiza bwanji? Kodi iye uja sabwera ku chikondwererochi?” 57 Apa n’kuti ansembe aakulu ndi Afarisi atalamula kuti aliyense amene angadziwe kumene kuli Yesu, aulule kuti iwo akamugwire.
12 Kutangotsala masiku 6 kuti pasika ayambike, Yesu anafika ku Betaniya+ kumene kunali Lazaro,+ uja amene Yesu anamuukitsa kwa akufa. 2 Choncho anamukonzera chakudya chamadzulo kumeneko, ndipo Marita+ anali kutumikira.+ Lazaro anali mmodzi wa anthu amene anali kudya naye.+ 3 Pamenepo Mariya anatenga mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado+ weniweni, okwera mtengo kwambiri okwana magalamu 327. Mariya anathira mafutawo pamapazi a Yesu ndi kupukuta mapaziwo ndi tsitsi lake.+ M’nyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafutawo. 4 Koma Yudasi Isikariyoti,+ mmodzi wa ophunzira ake, amene anali pafupi kumupereka anati: 5 “N’chifukwa chiyani mafuta onunkhirawa+ sanagulitsidwe madinari 300 ndi kupereka ndalamazo kwa anthu osauka?”+ 6 Koma iye ponena izi sikuti anali kudera nkhawa osauka ayi, koma chifukwa anali wakuba.+ Iye anali wosunga bokosi la ndalama,+ ndipo anali kutengamo ndalama zimene zinali kuponyedwa m’bokosilo. 7 Choncho Yesu anati: “M’lekeni, achite mwambo umenewu pokonzekera tsiku limene ndidzaikidwe m’manda.+ 8 Pakuti osaukawo+ muli nawo nthawi zonse, koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.”
9 Tsopano khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu ali kumeneko. Choncho linafika, osati chifukwa cha Yesu yekha ayi, komanso kuti lidzaone Lazaro, amene iye anamuukitsa kwa akufa.+ 10 Pamenepo ansembe aakulu anasonkhana pamodzi ndi kupangana zakuti aphenso Lazaro,+ 11 chifukwa Ayuda ambiri anali kupita kumeneko ndi kukhulupirira Yesu chifukwa cha Lazaroyo.+
12 Tsiku lotsatira, khamu lalikulu la anthu amene anabwera ku chikondwererocho, atamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemuko, 13 anatenga nthambi za kanjedza+ ndi kutuluka kukamuchingamira. Ndipo anayamba kufuula kuti:+ “M’pulumutseni!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova,+ amenenso ndi mfumu+ ya Isiraeli!” 14 Koma pamene Yesu anapeza bulu wamng’ono,+ anakwera pa iye monga mmene Malemba amanenera kuti: 15 “Usaope mwana wamkazi wa Ziyoni. Taona! Mfumu yako ikubwera.+ Ikubwera itakwera bulu wamng’ono wamphongo.”+ 16 Poyamba ophunzira akewo sanazindikire zimenezi.+ Koma pamene Yesu analandira ulemerero,+ iwo anakumbukira kuti zimenezi zinalembedwa ponena za iye. Anakumbukiranso kuti anamuchitira zimenezi.+
17 Tsopano anthu ambiri amene analipo pamene iye anaitana Lazaro+ kuti atuluke m’manda achikumbutso ndi kumuukitsa, anali kumuchitira umboni.+ 18 Pa chifukwa chimenechi, anthu onsewo anamuchingamira, chifukwa anamva kuti anachita chizindikiro+ chimenechi. 19 Pamenepo Afarisi+ anayamba kuuzana kuti: “Apa ndiye mukudzionera nokha kuti palibiretu chimene tikuphulapo. Onani! Dziko lonse lakhamukira kwa iye.”+
20 Pakati pa obwera kudzalambira ku chikondwereroko panalinso Agiriki.+ 21 Amenewa anafika kwa Filipo+ wa ku Betsaida ku Galileya, ndipo anayamba kumupempha kuti: “Bambo, ife tikufuna kuona Yesu.”+ 22 Filipo anapita kukauza Andireya zimenezo. Andireya ndi Filipo anapita kukauza Yesu.
23 Koma Yesu anawayankha kuti: “Nthawi yafika yakuti Mwana wa munthu alemekezedwe.+ 24 Ndithudi ndikukuuzani, Kambewu ka tirigu kakapanda kugwa m’nthaka ndi kufa, kamakhalabe kamodzi komweko. Koma kakafa,+ kamadzabala zipatso zambiri. 25 Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake+ m’dziko lino akuusungira moyo wosatha.+ 26 Ngati munthu wafuna kunditumikira ine, anditsatire, ndipo kumene ine ndidzakhala, mtumiki wanga adzakhalanso komweko.+ Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza.+ 27 Moyo wanga ukusautsika tsopano,+ ndinene chiyani kodi? Atate ndipulumutseni ku nthawi yosautsayi.+ Komabe nthawi imeneyi iyenera kundifikira pakuti ndiye chifukwa chake ndinabwera. 28 Atate lemekezani dzina lanu.” Pamenepo mawu+ anamveka kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”+
29 Chotero khamu la anthu amene anali ataimirira pamenepo ndi kumva zimenezi anayamba kunena kuti kwagunda bingu. Ena anayamba kunena kuti: “Mngelo walankhula naye.” 30 Poyankha Yesu anati: “Sikuti mawu amenewa amveka chifukwa cha ine ayi, koma chifukwa cha inu.+ 31 Tsopano dziko ili likuweruzidwa, wolamulira wa dzikoli+ aponyedwa kunja tsopano.+ 32 Koma ine ndikadzakwezedwa+ m’mwamba padziko lapansi, ndidzakokera anthu osiyanasiyana kwa ine.”+ 33 Kwenikweni ananena izi pofuna kusonyeza mtundu wa imfa imene anali pafupi kufa.+ 34 Pamenepo khamu la anthulo linamuyankha kuti: “Ife tinamva m’Chilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha.+ Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu adzakwezedwa m’mwamba?+ Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndani?”+ 35 Pamenepo Yesu anati: “Kuwala kukhalabe pakati panu kanthawi pang’ono. Yendani pamene kuwalako mudakali nako, kuti mdima+ usakugwereni, pakuti woyenda mu mdima sadziwa kumene akupita.+ 36 Pamene kuwala mudakali nako, sonyezani chikhulupiriro mwa kuwalako, kuti mukhale ana ake a kuwala.”+
Yesu atanena zimenezi, anachoka ndi kuwabisalira. 37 Koma ngakhale kuti anachita zizindikiro zambiri pamaso pawo, iwo sanali kukhulupirira iye, 38 moti mawu a mneneri Yesaya anakwaniritsidwa. Iye anati: “Yehova,* kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva?+ Ndipo kodi dzanja la Yehova laonetsedwa kwa ndani?”+ 39 Chifukwa chimene sanakhulupirire n’chimenenso Yesaya ananena kuti: 40 “Wachititsa khungu maso awo ndipo waumitsa mitima yawo,+ kuti asamaone ndi maso awowo, asazindikire ndi mitima yawo ndi kutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”+ 41 Yesaya ananena zimenezi chifukwa anaona ulemerero wa Khristu,+ ndipo ananena za iye. 42 Komabe ambiri, ngakhalenso olamulira anamukhulupirira,+ koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze poyera, poopa kuti angawachotse musunagoge.+ 43 Pakuti anakonda kwambiri ulemerero wa anthu kuposa ulemerero wa Mulungu.+
44 Koma Yesu anafuula kuti: “Wokhulupirira ine sakhulupirira ine ndekha, komanso amakhulupirira iye amene anandituma ine.+ 45 Amene wandiona ine waonanso amene anandituma.+ 46 Ndabwera monga kuwala m’dziko,+ kuti aliyense wokhulupirira ine asapitirize kukhala mumdima.+ 47 Ngati munthu wamva mawu anga koma osawasunga, ine sindiweruza woteroyo, pakuti sindinabwere kudzaweruza dziko,+ koma kudzalipulumutsa.+ 48 Aliyense wondinyalanyaza ndi kusalandira mawu anga, ali naye mmodzi womuweruza. Mawu+ amene ine ndalankhula ndi amene adzamuweruze pa tsiku lomaliza. 49 Chifukwa sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.+ 50 Komanso ndikudziwa kuti lamulo lake limatanthauza moyo wosatha.+ Choncho zimene ndimalankhula, monga mmene Atate anandiuzira, ndimazilankhula momwemo.”+
13 Tsopano Yesu anadziwiratu chikondwerero cha pasika chisanafike, kuti nthawi yake yochoka m’dzikoli kupita kwa Atate+ yakwana.+ Ndipo popeza kuti anali kuwakonda akewo amene anali m’dzikoli,+ anawakonda mpaka pa mapeto a moyo wake. 2 Chakudya chamadzulo chili mkati, Mdyerekezi anali ataika kale maganizo ofuna kupereka Yesu+ mumtima mwa Yudasi Isikariyoti,+ mwana wa Simoni. 3 Yesu anali kudziwa kuti Atate anapereka zinthu zonse m’manja mwake.+ Analinso kudziwa kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndi kuti anali kupita kwa Mulungu.+ 4 Choncho anaimirira pa chakudya chamadzulocho ndi kuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo ndi kumanga m’chiuno mwake.+ 5 Atatero anathira madzi m’beseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi+ a ophunzira ndi kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga m’chiuno lija. 6 Kenako anafika pa Simoni Petulo. Koma Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, inuyo mukufuna musambitse mapazi anga?”+ 7 Yesu anayankha kuti: “Zimene ndikuchitazi sungazimvetse padakali pano, koma pambuyo pake udzamvetsa.”+ 8 Petulo anati: “Ndithu, sizitheka kuti inu musambitse mapazi anga.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikapanda kukusambitsa,+ palibe chako kwa ine.” 9 Simoni Petulo anati: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, komanso manja ndi mutu womwe.” 10 Yesu anati: “Amene wasamba m’thupi+ amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.” 11 Iye anadziwa ndithu za munthu amene wakonza zomupereka.+ N’chifukwa chake ananena kuti: “Sikuti nonsenu ndinu oyera ayi.”
12 Tsopano atasambitsa mapazi awo ndi kuvalanso malaya ake akunja aja, anakhalanso patebulo. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa zimene ndachita kwa inu? 13 Inu mumanditcha kuti ‘Mphunzitsi’+ ndi ‘Ambuye,’+ mumalondola, pakuti ndinedi.+ 14 Choncho ngati ine, wokhala Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu,+ inunso muyenera kusambitsana mapazi.+ 15 Pakuti ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.+ 16 Ndithudi ndikukuuzani, Kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma.+ 17 Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.+ 18 Sindikunena nonsenu, ndikudziwa amene ndawasankha.+ Koma zili choncho kuti Malemba akwaniritsidwe,+ paja amati, ‘Munthu amene anali kudya chakudya changa wanyamula chidendene chake kundiukira.’+ 19 Kuyambira tsopano ndikukuuziranitu zisanachitike,+ kuti zikadzachitika mudzakhulupirire kuti ine ndinedi amene munali kumuyembekezera uja. 20 Ndithudi ndikukuuzani, Wolandira aliyense amene ine ndamutuma walandiranso ine.+ Ndipo amene walandira ine, walandiranso amene anandituma.”+
21 Atanena zimenezi, Yesu anasautsika mu mzimu, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Ophunzirawo anayamba kuyang’anizana posadziwa kuti anali kunena ndani.+ 23 Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anali kumukonda,+ anakhala patsogolo pa Yesu, pachifuwa chake. 24 Chotero Simoni Petulo anamukodola ndi mutu ndi kumuuza kuti: “Tiuze kuti akunena ndani.” 25 Pamenepo winayo anatsamira pachifuwa pa Yesu ndi kumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”+ 26 Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse chidutswa cha mkate chimene ndisunse.”+ Choncho atasunsa chidutswa cha mkate chija, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti. 27 Atamupatsa chidutswa cha mkatecho, pamenepo Satana analowa mwa Yudasi.+ Chotero Yesu anamuuza kuti: “Zimene wakonza kuchita, zichite mwamsanga.” 28 Koma panalibe aliyense mwa okhala patebulowo amene anadziwa chifukwa chimene anamuuzira zimenezi. 29 Popeza kuti Yudasi anali kusunga bokosi la ndalama,+ ena anali kuganiza kuti Yesu anali kumuuza kuti: “Ugule zofunikira zonse za chikondwerero,” kapena kuti apereke kenakake kwa osauka.+ 30 Choncho atalandira chidutswa cha mkate chija, anatuluka nthawi yomweyo. Umenewu unali usiku.+
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati: “Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa,+ ndipo Mulungu walemekezedwa kudzera mwa iye. 32 Mulungunso payekha amulemekeza iye,+ ndipo amulemekeza nthawi yomwe ino. 33 Ana apamtima inu,+ ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo monga ndinauzira Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’+ tsopano ndikuuzanso inuyo. 34 Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani,+ inunso muzikondana.+ 35 Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”+
36 Simoni Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire padakali pano, koma udzanditsatira m’tsogolo.”+ 37 Petulo anafunsanso kuti: “Ambuye, n’chifukwa chiyani sindingakutsatireni padakali pano? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”+ 38 Yesu anayankha kuti: “Kodi udzapereka moyo wako chifukwa cha ine? Ndithudi ndikukuuza iwe, Tambala asanalire undikana katatu.”+
14 “Mitima yanu isavutike.+ Khulupirirani Mulungu,+ khulupiriraninso ine.+ 2 M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambiri okhalamo.+ Akanapanda kukhalamo, ndikanakuuzani, chifukwa ndikupita kukakukonzerani malo.+ 3 Ndiponso, ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso+ kudzakutengerani kwathu,+ kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.+ 4 Ndipo kumene ndikupitako, inu njira yake mukuidziwa.”
5 Tomasi+ anafunsa kuti: “Ambuye, ife sitikudziwa kumene mukupita.+ Ndiye njira yake tingaidziwe bwanji?”
6 Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine njira,+ choonadi+ ndi moyo.+ Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.+ 7 Inu mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga. Kuyambira panopa mwawadziwa ndipo mwawaona.”+
8 Pamenepo Filipo anati: “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo tikhutira.”
9 Yesu anati: “Anthu inu, ndakhala nanu nthawi yonseyi, koma kodi iwe Filipo sunandidziwebe? Amene waona ine waonanso Atate.+ Nanga iwe bwanji ukunena kuti, ‘Tionetseni Atate’?+ 10 Sukukhulupirira kodi, kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana?+ Zinthu zimene ine ndimanena kwa inu sindilankhula za m’maganizo mwanga, koma Atate amene ali wogwirizana ndi ine ndiye akuchita ntchito zake.+ 11 Khulupirira kuti ine ndi Atate ndife ogwirizana, apo ayi, ingokhulupirira chifukwa cha ntchito zokhazi.+ 12 Ndithudi ndikukuuzani, Wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu+ kuposa zimenezi, chifukwa ine ndikupita kwa Atate.+ 13 Komanso chilichonse chimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzachichita, kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana wake.+ 14 Ngati mutapempha chilichonse m’dzina langa, ine ndidzachichita.
15 “Ngati mumandikonda, mudzasunga malamulo anga.+ 16 Inenso ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani mthandizi wina kuti adzakhale nanu kosatha.+ 17 Mthandizi ameneyo ndi mzimu wa choonadi.+ Mzimu umenewo dziko silingaulandire,+ chifukwa siliuona kapena kuudziwa. Inu mumaudziwa chifukwa umakhala mwa inu, ndipo uli mwa inu.+ 18 Sindikusiyani ngati ana amasiye.+ Ndidzabwera kwa inu. 19 Kwatsala kanthawi pang’ono ndipo dziko silidzandionanso.+ Koma inu mudzandiona,+ chifukwa ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.+ 20 Pa tsikulo mudzadziwa kuti ine ndili wogwirizana ndi Atate, inunso ndi ine ndife ogwirizana.+ 21 Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda.+ Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.”
22 Yudasi,+ wina osati Isikariyoti, anati: “Ambuye, bwanji mukufuna kudzionetsera bwinobwino kwa ife koma osati ku dzikoli?”+
23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga+ mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo tidzapita kwa iwo ndi kukakhala nawo.+ 24 Amene sandikonda ine sasunga mawu anga, ndipo mawu amene mukumvawa si anga, koma ndi a Atate amene anandituma.+
25 “Ndakuuzani zimenezi pamene ndidakali ndi inu. 26 Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.+ 27 Ndikusiyirani mtendere, ndikupatsani mtendere wanga.+ Sindikuupereka kwa inu mmene dziko limauperekera ayi. Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha. 28 Mwandimva ndikukuuzani kuti, Ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu. Ngati munali kundikonda, mukanakondwera kuti ndikupita kwa Atate wanga, chifukwa Atate ndi wamkulu+ kuposa ine. 29 Choncho, ndakuuzani zisanachitike,+ kuti zikachitika, mukhulupirire. 30 Sindilankhula nanunso zambiri, pakuti wolamulira+ wa dziko akubwera. Iye alibe mphamvu pa ine,+ 31 koma kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita izi kutsatira lamulo+ limene Atatewo anandipatsa. Nyamukani, tiyeni tichokeko kuno.
15 “Ine ndine mtengo wa mpesa weniweni,+ ndipo Atate wanga ndiye mlimi.+ 2 Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso amaidula,+ ndipo iliyonse yobala zipatso amaiyeretsa mwa kuitengulira+ kuti ibale zipatso zambiri.+ 3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ine ndalankhula kwa inu.+ 4 Khalani ogwirizana ndi ine, inenso ndikhala wogwirizana ndi inu.+ Nthambi singabale zipatso payokha, pokhapokha ngati ndi yolumikizikabe kumpesawo. Chimodzimodzi inunso, simungabale zipatso mukapanda kukhala olumikizika kwa ine.+ 5 Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake. Amene ali wolumikizika kwa ine, inenso n’kukhala wolumikizika kwa iye, ameneyo amabala zipatso zochuluka,+ chifukwa simungathe kuchita kalikonse popanda ine. 6 Ngati munthu sakhala wolumikizika kwa ine, amaponyedwa kunja monga nthambi ndipo amauma. Nthambi zoterozo anthu amazisonkhanitsa ndi kuziponya pamoto ndipo zimapsa.+ 7 Ngati mukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+ 8 Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri ndi kusonyeza kuti mulidi ophunzira anga.+ 9 Monga Atate wakondera ine,+ inenso kukonda inu, inunso khalanibe m’chikondi changa. 10 Mukasunga malamulo anga,+ mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate+ ndi kukhalabe m’chikondi chake.
11 “Ndalankhula zinthu izi kwa inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chisefukire.+ 12 Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukonderani.+ 13 Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.+ 14 Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.+ 15 Sindikutchanso inu kuti akapolo, chifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake amachita. Koma ndakutchani mabwenzi,+ chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.+ 16 Inu simunandisankhe ine, koma ine ndinakusankhani. Ndinakuikani kuti mupitirize kubala zipatso zochuluka,+ ndi kutinso zipatso zanuzo zisathe, kuti chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa akupatseni.+
17 “Ndikukulamulani zinthu izi, kuti muzikondana.+ 18 Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.+ 19 Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake.+ Koma popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+ 20 Kumbukirani mawu amene ndinakuuzani aja, kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.+ Ngati asunga mawu anga, adzasunganso anu. 21 Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.+ 22 Ndikanapanda kubwera kudzalankhula nawo, akanakhala opanda tchimo,+ koma tsopano alibe chodzilungamitsira pa tchimo lawo.+ 23 Wodana ndi ine amadananso ndi Atate wanga.+ 24 Ndikanapanda kuchita pakati pawo ntchito zimene wina aliyense sanachitepo,+ akanakhala opanda tchimo,+ koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga.+ 25 Zili choncho kuti mawu olembedwa m’Chilamulo akwaniritsidwe. Mawu ake ndi akuti, ‘Anadana nane popanda chifukwa.’+ 26 Akadzafika mthandizi amene ndidzamutumiza kuchokera kwa Atate,+ amene ndi mzimu wa choonadi wochokera kwa Atate, ameneyo adzandichitira umboni,+ 27 ndipo inunso mudzachitira umboni,+ chifukwa mwakhala nane kuchokera pa chiyambi.
16 “Ndalankhula zimenezi kwa inu kuti musapunthwe.+ 2 Anthu adzakuchotsani m’sunagoge.+ Ndipo nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu.+ 3 Koma adzachita zimenezi chifukwa sanadziwe Atate kapena ine.+ 4 Ine ndalankhula zinthu zimenezi kwa inu, kuti nthawi yake ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndinakuuzani zimenezi.+
“Zinthu izi sindinakuuzeni pa chiyambi pomwe, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu. 5 Koma tsopano ndikupita kwa amene anandituma,+ ndipo palibe aliyense wa inu amene akundifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’ 6 Koma chifukwa ndalankhula zimenezi kwa inu, chisoni+ chadzaza m’mitima yanu. 7 Koma kunena zoona, ndikupita kuti inu mupindule. Pakuti ngati sindipita, ndiye kuti mthandizi+ uja sabwera kwa inu. Koma ndikapita, ndikamutumiza kwa inu. 8 Ndipo iye akadzafika adzapereka umboni wotsimikizika ku dzikoli wonena za tchimo, za chilungamo, ndi za chiweruzo.+ 9 Koma choyamba adzapereka umboni wonena za tchimo,+ chifukwa iwo sakundikhulupirira.+ 10 Kenako adzapereka umboni wonena za chilungamo,+ chifukwa ine ndikupita kwa Atate ndipo inu simudzandionanso. 11 Pomaliza adzapereka umboni wonena za chiweruzo,+ chifukwa wolamulira wa dziko lino waweruzidwa.+
12 “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.+ 13 Koma mthandiziyo akadzafika, amene ndi mzimu wa choonadi,+ adzakutsogolerani m’choonadi chonse. Pakuti sadzalankhula zongoganiza mwa iye yekha, koma adzalankhula zimene wazimva, ndipo adzalengeza kwa inu zinthu zimene zikubwera.+ 14 Iyeyo adzandilemekeza,+ chifukwa adzalandira za ine ndipo adzazilengeza kwa inu.+ 15 Zonse zimene Atate ali nazo ndi zanga.+ N’chifukwa chake ndikunena kuti adzalandira za ine ndi kuzilengeza kwa inu. 16 Kwa kanthawi simudzandionanso,+ ndipo kwa kanthawi mudzandiona.”
17 Pamenepo ena mwa ophunzira akewo anayamba kufunsana kuti: “Kodi akutanthauza chiyani mmene akutiuza kuti, ‘Kwa kanthawi simudzandionanso, ndipo kwa kanthawi mudzandiona,’ ndi kuti, ‘chifukwa ndikupita kwa Atate’?” 18 Kwenikweni anali kunena kuti: “Kodi akutanthauza chiyani mmene akuti, ‘kwa kanthawi’? Sitikudziwa zimene akunena.” 19 Yesu anadziwa+ kuti akufuna kumufunsa, choncho iye anawafunsa kuti: “Kodi mukufunsana nokhanokha zimenezi, chifukwa ndanena kuti, Kwa kanthawi simudzandiona, ndipo kwa kanthawi mudzandiona? 20 Ndithudi ndikukuuzani, Mudzagwetsa misozi ndi kulira mofuula, koma dzikoli lidzasangalala. Mudzamva chisoni,+ koma chisoni chanu adzachisandutsa chimwemwe.+ 21 Pamene mayi akubereka amazunzika kwambiri, chifukwa nthawi yake yafika.+ Koma mwana akabadwa, sakumbukiranso kupweteka konse kuja chifukwa cha chimwemwe kuti munthu wabadwa padziko. 22 Choncho inunso muli ndi chisoni panopa. Koma ndidzakuonaninso, ndipo mitima yanu idzasangalala.+ Palibenso amene adzathetse chimwemwe chanu. 23 Pa tsiku limenelo+ simudzandifunsanso mafunso. Ndithudi ndikukuuzani, Ngati mupempha chilichonse+ kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.+ 24 Kufikira nthawi ino simunapemphepo chilichonse m’dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chisefukire.+
25 “Ndalankhula zimenezi kwa inu m’mafanizo.+ Nthawi ikubwera pamene sindidzalankhulanso ndi inu m’mafanizo, koma ndidzakuuzani za Atate m’njira yosavuta kumva. 26 Pa tsikulo mudzapempha m’dzina langa, sindikunena kuti ndidzakupempherani kwa Atate ayi. 27 Pakuti Atateyo amakukondani, chifukwa munandikonda+ ine ndipo mwakhulupirira kuti ine ndinabwera monga nthumwi ya Atate.+ 28 Ndinachokera kwa Atate ndipo ndinabwera m’dziko. Tsopano ndikuchoka m’dziko kupita kwa Atate.”+
29 Ophunzira akewo anati: “Eya! Tsopano mukulankhula m’njira yosavuta kumva, ndipo simukulankhulanso mwa mafanizo. 30 Tadziwa tsopano kuti inu mukudziwa zonse+ ndipo m’posafunikanso kuti munthu akufunseni mafunso.+ Pa chifukwa chimenechi tikukhulupirira kuti munachokeradi kwa Mulungu.”+ 31 Yesu anawayankha kuti: “Kodi panopa mukukhulupirira? 32 Taonani! Nthawi ikubwera, ndipo yafika kale. Mubalalika aliyense kupita kunyumba kwake,+ ndipo mundisiya ndekha. Koma sindikhala ndekha, chifukwa Atate ali ndi ine.+ 33 Ndanena zimenezi kwa inu kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine.+ M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”+
17 Yesu atalankhula zinthu zimenezi, anakweza maso ake kumwamba+ ndi kunena kuti: “Atate, nthawi yafika, lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.+ 2 Inu mwamupatsa ulamuliro pa anthu onse,+ kuti onse amene inu mwamupatsa,+ awapatse moyo wosatha.+ 3 Pakuti moyo wosatha+ adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa+ za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona,+ ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.+ 4 Ndakulemekezani+ padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa.+ 5 Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.+
6 “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu.+ Anali anu, koma munawapereka kwa ine, ndipo iwo asunga mawu anu. 7 Tsopano adziwa kuti zonse zimene munandipatsa n’zochokera kwa inu, 8 chifukwa mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo.+ Iwo awalandira ndipo adziwa ndithu kuti ine ndinabwera monga nthumwi yanu,+ ndipo akhulupirira kuti ndinu amene munandituma.+ 9 Choncho ndikupempha m’malo mwa iwo, sindikupemphera dziko,+ koma awo amene mwandipatsa, chifukwa iwo ndi anu. 10 Zonse zimene ndili nazo ndi zanu ndipo zanu zonse ndi zanga.+ Ine ndalemekezeka pakati pawo.
11 “Komanso, ine sindikhalanso m’dzikoli pakuti ndikubwera kwa inu, koma iwo adakali m’dzikoli.+ Atate Woyera, ayang’anireni+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi mmene ife tilili.+ 12 Pamene ndinali nawo pamodzi, ndinali kuwayang’anira+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa. Ine ndawasunga moti palibe aliyense wa iwo amene wawonongeka+ kupatulapo mwana wa chiwonongeko,+ kuti malemba akwaniritsidwe.+ 13 Koma tsopano ndikubwera kwa inu, ndipo ndikulankhula zimenezi pamene ndili m’dziko kuti akhale ndi chimwemwe chosefukira ngati chimene ine ndili nacho.+ 14 Iwo ndawapatsa mawu anu, koma dziko likudana nawo,+ chifukwa sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.+
15 “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo.+ 16 Iwo sali mbali ya dziko,+ monganso ine sindili mbali ya dziko.+ 17 Ayeretseni+ ndi choonadi. Mawu+ anu ndiwo choonadi.+ 18 Monga mmene munanditumizira ine m’dziko, inenso ndawatumiza m’dziko.+ 19 Ndipo ine ndikudziyeretsa chifukwa cha iwo, kuti iwonso ayeretsedwe+ ndi choonadi.
20 “Sindikupemphera awa okha, komanso amene amakhulupirira ine kudzera m’mawu awo,+ 21 kuti onsewa akhale amodzi,+ mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana,+ kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife,+ ndi kuti dziko likhulupirire kuti inu munanditumadi.+ 22 Komanso, ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa, kuti iwo akhale amodzi mmene ifenso tilili amodzi.+ 23 Ine wogwirizana ndi iwo, inu wogwirizana ndi ine, kuti iwo akhale mu umodzi weniweni,+ kuti dziko lidziwe kuti inu munandituma ine, ndi kuti munawakonda iwo mmene munandikondera ine. 24 Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale,+ kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko+ a dziko.+ 25 Atate wolungama,+ ndithudi dziko silinakudziweni,+ koma ine ndikukudziwani ndipo awa adziwa kuti inu munandituma.+ 26 Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu+ ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”+
18 Atanena zimenezi, Yesu anatuluka pamodzi ndi ophunzira ake ndi kuwoloka khwawa la Kidironi,+ kupita kumene kunali munda. Ndipo iye ndi ophunzira akewo analowa m’mundamo.+ 2 Yudasi womupereka uja, analinso kuwadziwa malowo, chifukwa nthawi zambiri Yesu anali kukumana ndi ophunzira ake kumeneko.+ 3 Choncho Yudasi anatenga gulu la asilikali ndi alonda ochokera kwa ansembe aakulu ndi kwa Afarisi. Iwo anafika kumeneko atanyamula miyuni, nyale ndi zida.+ 4 Chotero Yesu, podziwa zonse zimene zinali pafupi kumuchitikira,+ anawayandikira ndi kuwafunsa kuti: “Mukufuna ndani?” 5 Iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.”+ Iye anati: “Ndine amene.” Yudasi womupereka uja,+ analinso nawo pamenepo.
6 Koma pamene anawauza kuti: “Ndine amene,” iwo anafutuka+ ndi kugwa pansi. 7 Kenako anawafunsanso kuti: “Mukufuna ndani?” Iwo anati: “Yesu Mnazareti.” 8 Yesu anati: “Ndakuuzani kuti ndine amene. Choncho ngati mukufuna ine, awa alekeni azipita,” 9 kuti mawu amene iye ananena akwaniritsidwe, akuti: “Mwa onse amene munandipatsa sindinatayepo ngakhale mmodzi.”+
10 Pamenepo Simoni Petulo, popeza anali ndi lupanga, analisolola ndi kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe ndi kuduliratu khutu lake lakumanja.+ Dzina la kapoloyo anali Makasi. 11 Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezera lupangalo m’chimake.+ Kodi sindiyenera kumwa za m’kapu imene Atate wandipatsa,+ zivute zitani?”
12 Pamenepo gulu la asilikali lija, mkulu wa asilikali ndi alonda a Ayuda anagwira Yesu ndi kumumanga. 13 Choyamba anapita naye kwa Anasi, pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho.+ 14 Kayafa ameneyu ndi amene analangiza Ayuda uja kuti kunali kopindulitsa kwa iwo kuti munthu mmodzi afere anthu onse.+
15 Tsopano Simoni Petulo ndiponso wophunzira wina anali kutsatira Yesu.+ Wophunzira winayu anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, chotero analowa pamodzi ndi Yesu m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe. 16 Koma Petulo anaimirira kunja pakhomo.+ Choncho wophunzira winayu, amene anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe uja, anapita kukalankhula ndi mlonda wa pakhomo ndipo analowetsa Petulo. 17 Pamenepo mtsikana wantchito, amene anali mlonda wa pakhomopo, anafunsa Petulo kuti: “Kodi inunso si inu mmodzi wa ophunzira a munthu ameneyu?” Iye anati: “Ayi si ine.”+ 18 Akapolo ndi alonda anali ataima chapomwepo, pakuti anali atakoleza moto wamakala,+ chifukwa kunali kuzizira ndipo anali kuwotha motowo. Nayenso Petulo anaimirira pamodzi ndi iwo n’kumawotha nawo.
19 Ndiyeno wansembe wamkulu uja anafunsa Yesu za ophunzira ake ndi za chiphunzitso chake. 20 Yesu anamuyankha kuti: “Ndalankhula poyera ku dzikoli. Nthawi zonse ndinali kuphunzitsa m’masunagoge ndi m’kachisi,+ kumene Ayuda onse anali kusonkhana, ndipo sindinalankhule kanthu mseri. 21 N’chifukwa chiyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinali kunena kwa iwo. Onani! Onsewa akudziwa zimene ndinali kunena.” 22 Atanena zimenezi, mmodzi wa alonda amene anaimirira chapafupi anamenya Yesu mbama,+ ndi kunena kuti: “Ungamuyankhe choncho wansembe wamkulu?” 23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati ndalankhula molakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati ndalankhula moyenera, n’chifukwa chiyani ukundimenya?” 24 Kenako Anasi anatumiza Yesu ali womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe.+
25 Pa nthawiyi Simoni Petulo anali ataimirira akuwotha moto. Pamenepo iwo anamufunsa kuti: “Kodi iwenso si iwe mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anakana n’kunena kuti: “Ayi si ine.”+ 26 Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, amenenso anali wachibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu uja,+ anati: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” 27 Koma Petulo anakananso. Nthawi yomweyo tambala analira.+
28 Ndiyeno iwo anatenga Yesu kuchoka kwa Kayafako ndi kupita naye kunyumba ya bwanamkubwa.+ Umenewu unali m’mawa kwambiri. Koma iwo sanalowe m’nyumba ya bwanamkubwayo poopa kuipitsidwa.+ Iwo anali kufuna kuti akathe kudya pasika. 29 Choncho Pilato anatuluka ndi kuwafunsa kuti: “Kodi mukumuimba mlandu wanji munthu ameneyu?”+ 30 Iwo anayankha kuti: “Munthu uyu akanakhala wosachita zoipa, sitikanabwera naye kwa inu.” 31 Pamenepo Pilato anati: “M’tengeni eniakenu mukamuweruze mogwirizana ndi chilamulo chanu.”+ Ayudawo anati: “N’zosaloleka kwa ife kupha munthu aliyense.”+ 32 Zinali choncho kuti mawu a Yesu akwaniritsidwe. Mawuwo anawanena pofuna kusonyeza mtundu wa imfa imene iye amayembekezeka kufa.+
33 Choncho Pilato analowanso m’nyumba ya bwanamkubwa n’kuitana Yesu ndi kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?”+ 34 Yesu anayankha kuti: “Kodi zimenezi mukunena nokha, kapena ena akuuzani za ine?”+ 35 Pilato anayankha kuti: “Kodi ine ndine Myuda ngati? Anthu a mtundu wako omwe ndi ansembe aakulu ndi amene akupereka kwa ine.+ Kodi unachita chiyani?” 36 Yesu anayankha kuti:+ “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.+ Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo+ kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” 37 Pamenepo Pilato anati: “Chabwino, koma kodi ndiwe mfumu?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu.+ Chimene ndinabadwira, ndiponso chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.+ Aliyense amene ali kumbali ya choonadi+ amamvera mawu anga.”+ 38 Pilato anafunsa kuti: “Choonadi n’chiyani?”
Atangofunsa funso limeneli, anatuluka ndi kupitanso kumene kunali Ayuda kuja, ndi kuwauza kuti: “Ineyo sindikupeza cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu.+ 39 Pajanso inu muli ndi mwambo wakuti ndizikumasulirani munthu mmodzi pa pasika.+ Kodi mukufuna ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” 40 Pamenepo iwo anafuulanso kuti: “Ameneyo ayi, koma Baraba!” Koma Baraba ameneyu anali wachifwamba.+
19 Tsopano Pilato anatenga Yesu ndi kumukwapula.+ 2 Ndipo asilikali analuka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka kumutu. Anamuvekanso malaya akunja ofiirira.+ 3 Pamenepo anayamba kubwera kwa iye ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu, inu Mfumu ya Ayuda!” Komanso anali kumumenya mapama.+ 4 Pilato anatulukanso kunja ndi kuwauza kuti: “Onani! Ndikumutulutsa panja pano kwa inu, kuti mudziwe kuti sindikupeza mlandu mwa iye.”+ 5 Pamenepo Yesu anatulukira panja, atavala chisoti chachifumu chaminga chija ndi malaya akunja ofiirira. Ndipo Pilato anati: “Taonani! Mwamuna uja ndi uyu!” 6 Koma pamene ansembe aakulu ndi alonda anamuona, anafuula kuti: “M’pachikeni! M’pachikeni!”+ Pilato anawauza kuti: “M’tengeni mukamupachike nokha, chifukwa ine sindikupeza mlandu uliwonse mwa iye.”+ 7 Ayudawo anamuyankha kuti: “Tili ndi chilamulo ife,+ ndipo malinga ndi chilamulocho iyeyu ayenera kufa, chifukwa akudziyesa mwana wa Mulungu.”+
8 Choncho Pilato atamva mawu amenewa, anachita mantha kwambiri. 9 Analowanso m’nyumba ya bwanamkubwa ndi kufunsa Yesu kuti: “Kodi umachokera kuti?” Koma Yesu sanamuyankhe.+ 10 Pamenepo Pilato anati: “Kodi sukundilankhula?+ Kodi sukudziwa kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula, komanso yokupachika?” 11 Yesu anamuyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba.+ Ndiye chifukwa chake munthu amene wandipereka ine kwa inu ali ndi tchimo lalikulu kwambiri.”
12 Pa chifukwa chimenechi Pilato anayesetsabe kufunafuna njira kuti amumasule. Koma Ayudawo anafuula kuti: “Mukamumasula ameneyu, ndiye kuti si inu bwenzi la Kaisara. Munthu aliyense wodziyesa yekha mfumu, ameneyo ndi wotsutsana ndi Kaisara.”+ 13 Choncho pamene Pilato anamva mawu amenewa, anatulutsa Yesu panja, ndipo iye anakhala pampando woweruzira milandu, pamalo otchedwa Bwalo Lamiyala, koma pa Chiheberi otchedwa Gabʹba·tha. 14 Ili linali tsiku lokonzekera+ pasika, ndipo nthawi inali cha m’ma 12 koloko masana.* Pamenepo iye anauza Ayudawo kuti: “Taonani! Mfumu yanu imeneyi!” 15 Koma iwo anafuula kuti: “Muthane naye! Muthane naye! M’pachikeni!” Pilato anawafunsa kuti: “Kodi ndipachike mfumu yanu?” Ansembe aakulu anayankha kuti: “Tilibe mfumu ina koma Kaisara.”+ 16 Pamenepo anamupereka kwa iwo kuti akamupachike.+
Tsopano Yesu anakhala m’manja mwawo. 17 Ndipo iye ananyamula yekha mtengo wozunzikirapo*+ ndi kutuluka+ kupita kumalo otchedwa Chibade, koma pa Chiheberi otchedwa, Gologota.+ 18 Kumeneko anamupachika+ pamodzi ndi amuna ena awiri, wina mbali iyi, wina mbali inayi, Yesu pakati.+ 19 Pilato analembanso dzina laudindo ndi kuliika pamtengo wozunzikirapowo. Analemba kuti: “Yesu Mnazareti, Mfumu ya Ayuda.”+ 20 Choncho Ayuda ambiri anawerenga dzina laudindo limeneli, chifukwa malo amene Yesu anapachikidwa anali pafupi ndi mzinda,+ ndipo analilemba m’Chiheberi, Chilatini, ndi Chigiriki. 21 Koma ansembe aakulu a Ayudawo anayamba kuuza Pilato kuti: “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti iye ananena kuti, ‘Ndine Mfumu ya Ayuda.’” 22 Pilato anayankha kuti: “Zimene ndalemba, ndalemba.”
23 Tsopano asilikaliwo atamupachika Yesu, anatenga malaya ake akunja ndi kuwagawa m’zigawo zinayi, kuti msilikali aliyense atenge chigawo chimodzi. Panalinso malaya amkati. Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anali owombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ 24 Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Malaya awa tisawang’ambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.” Izi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, limene linati: “Iwo anagawana malaya anga akunja pakati pawo, ndipo anachita maere pa malaya anga amkati.”+ Chotero asilikaliwo anachitadi zimenezi.
25 Koma chapafupi ndi mtengo wozunzikirapo wa Yesu, panaimirira mayi ake+ ndi m’bale wa mayi akewo, Mariya+ mkazi wa Kulopa, ndi Mariya Mmagadala.+ 26 Choncho Yesu, poona mayi akewo ndi wophunzira amene anali kumukonda+ uja ataima chapafupi, anauza mayi akewo kuti: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.” 27 Kenako anauza wophunzirayo kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.” Ndipo kuyambira nthawi imeneyo wophunzirayo anatenga mayiwo ndi kupita nawo kunyumba kwake.
28 Pambuyo pake, Yesu atadziwa kuti tsopano zonse zachitika, kuti malemba akwaniritsidwe anati: “Ndikumva ludzu.”+ 29 Pamalopo panali chiwiya chodzaza vinyo wowawasa. Pamenepo anatenga chinkhupule chimene anachiviika m’vinyo wowawasayo n’kuchisomeka kukamtengo ka hisope ndi kuchifikitsa pakamwa pake.+ 30 Atalandira vinyo wowawasayo, Yesu anati: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”+ ndipo anaweramitsa mutu, ndi kupereka mzimu wake.+
31 Popeza linali Tsiku Lokonzekera,+ Ayudawo sanafune kuti mitembo ikhalebe+ pamitengo yozunzikirapo tsiku la Sabata, (pakuti Sabata la tsiku limeneli linali lalikulu,)+ choncho anapempha Pilato kuti opachikidwawo awathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo. 32 Chotero asilikali anafika ndi kuthyola miyendo ya munthu woyamba ndiponso ya wina uja amene anapachikidwa naye pamodzi. 33 Koma atafika pa Yesu, sanamuthyole miyendo poona kuti wafa kale. 34 Koma mmodzi wa asilikaliwo anamulasa ndi mkondo m’mbalimu cham’mimba,+ ndipo nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi. 35 Munthu amene anaona zimenezo akuchitira umboni, ndipo umboni wakewo ndi woona. Munthu ameneyu akudziwa kuti amanena zoona, kuti inunso mukhulupirire.+ 36 Kwenikweni izi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, pamene linati: “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.”+ 37 Ndiponso lemba lina limati: “Iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa.”+
38 Tsopano zitatha izi, Yosefe wa ku Arimateya, amene anali wophunzira wa Yesu koma wamseri chifukwa anali kuopa Ayuda,+ anapempha Pilato kuti amulole kuti akachotse mtembo wa Yesu, ndipo Pilato anamupatsa chilolezo.+ Choncho anafika ndi kuchotsa mtembowo.+ 39 Nayenso Nikodemo, munthu amene anabwera kwa iye usiku poyamba paja, anabwera atatenga mule wosakaniza ndi aloye, wopitirira makilogalamu 32.+ 40 Choncho iwo anatenga mtembo wa Yesu n’kuukulunga ndi nsalu zamaliro zonunkhira,+ malinga ndi mwambo umene Ayuda anali kutsatira poika maliro. 41 Tsopano kumalo kumene anamupachikirako kunali munda. M’munda umenewo munali manda achikumbutso+ atsopano, mmene anali asanaikemo munthu chikhalire. 42 Choncho, popeza linali tsiku lokonzekera+ chikondwerero cha Ayuda, iwo anaika Yesu mmenemo, chifukwa manda achikumbutsowo anali pafupi.
20 Tsiku loyamba+ la mlunguwo, Mariya Mmagadala anabwera kumanda achikumbutsowo m’mawa kwambiri, kudakali mdima, ndipo anaona kuti mwala wachotsedwa kale pamanda achikumbutsowo.+ 2 Pamenepo iye anathamanga ndi kukafika kwa Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina,+ amene Yesu anali kumukonda kwambiri uja. Iye anawauza kuti: “Ambuye awachotsa m’manda achikumbutso+ aja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.”
3 Pamenepo Petulo+ ndi wophunzira wina uja ananyamuka kupita kumanda achikumbutsowo. 4 Onse awiri anayambira pamodzi kuthamanga, koma wophunzira winayo anapitirira Petulo ndi liwiro lalikulu ndipo anali woyambirira kukafika kumanda achikumbutsowo. 5 Atawerama ndi kuyang’anitsitsa, anangoona nsalu zokulungira mtembo zokha zija zili pansi,+ koma sanalowe mkatimo. 6 Kenako Simoni Petulo anafikanso m’mbuyo mwake, ndipo analowa m’manda achikumbutsowo. Mmenemo anaona nsalu zokulungira mtembozo zili pansi.+ 7 Anaonanso nsalu ina imene anamukulungira kumutu ataipindapinda ndi kuiika payokha. Imeneyi sinaikidwe pamodzi ndi nsalu zokulungira mtembozo. 8 Pamenepo, wophunzira winayo, amene anali woyambirira kufika kumanda achikumbutso uja analowanso mkatimo, ndipo anaona ndi kukhulupirira zimene Mariya anawauza. 9 Iwo anali asanazindikire malemba akuti Yesu ayenera kuuka kwa akufa.+ 10 Pamenepo ophunzirawo anabwerera kunyumba kwawo.
11 Koma Mariya anatsala atangoima panja pafupi ndi manda achikumbutsowo akulira. Akulira choncho, anawerama kuti aone m’manda achikumbutsowo. 12 Atatero, anaona angelo awiri+ ovala zoyera, mmodzi atakhala pansi kumutu, winanso atakhala pansi kumiyendo, pamalo amene panagona mtembo wa Yesu. 13 Iwo anamufunsa kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira?” Iye anati: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.” 14 Atanena zimenezi, anatembenuka ndi kuona Yesu ali chilili, koma sanam’zindikire kuti ndi Yesu.+ 15 Ndiyeno Yesu anafunsa mayiyo kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira? Kodi Ukufuna ndani?”+ Poganiza kuti ndi wosamalira mundawo, iye anamuyankha kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika, ndipo ine ndikamutenga.” 16 Pamenepo Yesu anati: “Mariya!”+ Pamene anatembenuka, ananena kwa iye m’Chiheberi kuti: “Rab·boʹni!”+ (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”) 17 Yesu anati: “Usandikangamire. Pakuti sindinakwerebe kwa Atate. Koma pita kwa abale anga+ ukawauze kuti, ‘Ine ndikukwera kwa Atate+ wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga+ ndi Mulungu wanu.’”+ 18 Mariya Mmagadala anafika ndi kuuza ophunzira uthengawo. Anati: “Ambuye ndawaona ine!” Ndipo anawauza zimene iye anamuuza zija.+
19 Pa tsiku limenelo, tsiku loyamba la mlunguwo,+ ophunzirawo anasonkhana pamodzi madzulo. Iwo anali atakhoma zitseko m’nyumba imene analimo chifukwa choopa+ Ayuda, ndipo Yesu anafika+ n’kuimirira pakati pawo ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 20 Atanena zimenezi, anawaonetsa manja ake ndi pambali pa mimba paja.+ Pamenepo ophunzirawo anasangalala+ poona Ambuyewo. 21 Kenako Yesu anawauzanso kuti: “Mtendere ukhale nanu. Mmene Atate ananditumira,+ inenso ndikutumani.”+ 22 Atanena zimenezi, anauzira mpweya pa iwo ndi kuwauza kuti: “Landirani mzimu woyera.+ 23 Mukakhululukira munthu amene wachita tchimo,+ ndiye kuti Mulungu wamukhululukira kale. Koma mukapanda kukhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukire.”+
24 Koma Tomasi,+ wotchedwa Didimo, mmodzi wa ophunzira 12 aja sanali pamodzi nawo pamene Yesu anafika. 25 Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anati: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo,+ ine sindikhulupirira ayi.”+
26 Tsopano patapita masiku 8, ophunzira akewo analinso m’nyumba, ndipo Tomasi anali nawo pamodzi. Yesu anafika ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma. Iye anaimirira pakati pawo ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 27 Kenako anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa, ndiponso ona m’manja mwangamu. Gwiranso ndi dzanja lako+ m’mbali mwa mimba yangamu, kuti usakhalenso wosakhulupirira, koma wokhulupirira.” 28 Poyankha Tomasi anati: “Mbuyanga ndi Mulungu wanga!”+ 29 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Odala ndi amene amakhulupirira ngakhale sanaone.”+
30 Kunena zoona, Yesu anachita zizindikiro zinanso zambiri pamaso pa ophunzirawo, zimene sizinalembedwe mumpukutu uno.+ 31 Koma izi zalembedwa+ kuti mukhulupirire kuti Yesu alidi Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kutinso, mwa kukhulupirira,+ mukhale ndi moyo m’dzina lake.
21 Zimenezi zitatha, Yesu anaonekeranso kwa ophunzirawo kunyanja ya Tiberiyo.* Kuonekera kwakeko kunali motere. 2 Simoni Petulo, Tomasi wotchedwa Didimo,+ Natanayeli+ wa ku Kana wa m’Galileya, ana a Zebedayo,+ ndi ophunzira ake ena awiri anali pamodzi. 3 Ndiyeno Simoni Petulo anati: “Ine ndikupita kukapha nsomba.” Enawonso anati: “Ifenso tipita nawe.” Iwo anapitadi ndi kukwera ngalawa, koma mkati mwa usiku umenewo sanaphe kanthu.+
4 Pamene kunali kucha, Yesu anaimirira m’mbali mwa nyanja, koma ophunzirawo sanazindikire kuti anali Yesu.+ 5 Kenako Yesu anati: “Ana inu, kodi muli ndi chakudya chilichonse?” Iwo anamuyankha kuti, “Ayi!” 6 Iye anati: “Ponyani ukonde kumbali ya kudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.”+ Pamenepo anaponyadi ukondewo, koma sanathenso kuukoka chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.+ 7 Zitatero, wophunzira amene Yesu anali kumukonda kwambiri uja+ anauza Petulo+ kuti: “Ndi Ambuye!” Pamenepo Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala malaya ake ovala pamwamba, pakuti anali maliseche,* ndipo analumphira m’nyanja. 8 Koma ophunzira enawo anabwera m’ngalawa yaing’ono akukoka ukonde wa nsomba, pakuti sanali patali kwenikweni ndi kumtunda. Anali pa mtunda wa mamita pafupifupi 90 okha.
9 Tsopano atafika kumtunda anaona moto wamakala+ uli potero pali nsomba, ndipo anaonanso mkate. 10 Yesu anati: “Bweretsani kuno zina mwa nsomba zimene mwaphazo.” 11 Choncho Simoni Petulo analowa m’ngalawamo ndi kukokera kumtunda ukonde wodzala nsomba zikuluzikulu zokwana 153. Koma ngakhale kuti munali nsomba zochuluka choncho, ukondewo sunang’ambike. 12 Yesu anawauza kuti: “Bwerani mudzadye chakudya cham’mawa.”+ Panalibe ngakhale mmodzi mwa ophunzirawo amene analimba mtima kumufunsa kuti: “Ndinu ndani?” chifukwa anali kudziwa kuti ndi Ambuye. 13 Yesu anapita kukatenga mkate ndi kuwagawira,+ chimodzimodzinso ndi nsomba. 14 Kameneka kanali kachitatu+ kwa Yesu kuonekera kwa ophunzira akewo pambuyo pakuti waukitsidwa kwa akufa.
15 Atatsiriza kudya chakudya cham’mawacho, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?”+ Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.”+ Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.”+ 16 Kenako anamufunsa kachiwiri kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?”+ Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, mukudziwa inunso kuti ndimakukondani kwambiri.” Pamenepo anati: “Weta ana a nkhosa anga.”+ 17 Anamufunsanso kachitatu: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda kwambiri?” Petulo anamva chisoni kumva akumufunsa kachitatu kuti: “Kodi ine umandikonda kwambiri?” Choncho iye anati: “Ambuye, inu mumadziwa zonse,+ mukudziwanso bwino kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anati: “Dyetsa ana a nkhosa anga.+ 18 Ndithudi ndikukuuza iwe, Pamene unali mnyamata, unali kuvala wekha ndi kupita kumene unali kufuna. Koma ukadzakalamba, udzatambasula manja ako ndipo munthu wina adzakuveka,+ ndi kukunyamula kupita nawe kumene iwe sukufuna.”+ 19 Ananena zimenezi pofuna kusonyeza mtundu wa imfa+ imene adzalemekeza nayo Mulungu.+ Choncho atanena zimenezi, anamuuza kuti: “Pitiriza kunditsatira.”+
20 Petulo atatembenuka, anaona wophunzira amene Yesu anali kumukonda+ akuwalondola. Wophunzira ameneyu ndi amene pa chakudya chamadzulo chija anatsamira pachifuwa cha Yesu ndi kumufunsa kuti: “Ambuye, ndani amene akufuna kukuperekani?” 21 Pamene anamuona, Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, nanga uyu adzachita chiyani?” 22 Yesu anati: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe kufikira ndikadzabwera,+ kodi iwe uli nazo kanthu? Iweyo ungopitiriza kunditsatira.” 23 Atanena choncho, mawu amenewa anafalikira mwa abale, kuti wophunzira ameneyu sadzamwalira. Koma Yesu sanamuuze kuti sadzamwalira, koma ananena kuti: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe+ kufikira ndikadzabwera, kodi iwe uli nazo kanthu?”
24 Wophunzira ameneyu+ ndiye akuchitira umboni zinthu zimenezi. Iyeyu ndi amenenso analemba zinthu zimenezi, ndipo tikudziwa kuti umboni umene akupereka ndi woona.+
25 Ndipo pali zinthu zinanso zambiri zimene Yesu anachita. Zikanakhala kuti zonse zinalembedwa mwatsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana m’dzikoli.+
“Wonga mulungu, waumulungu.” Onani Zakumapeto 10.
Mawu ake enieni, “ola la 10,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
Mawu ake enieni, “ola la 7,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
M’Baibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, “nyanja ya Kinereti,” “nyanja ya Genesarete,” komanso “nyanja ya Tiberiyo.”
Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 7.
Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”
Onani Zakumapeto 2.
Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Onani Zakumapeto 9.
M’Baibulo, “nyanja ya Tiberiyo” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete, komanso nyanja ya Galileya.
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “ali maliseche,” angatanthauze kuti “asanavale mokwanira” kapena “atavala zovala zamkati zokha,” osati ali mbulanda kapena asanavale chilichonse.