Machitidwe a Atumwi
1 A Teofilo,+ m’nkhani yoyamba ija, ndinalemba zonse zimene Yesu anali kuchita ndi kuphunzitsa kuchokera pa chiyambi,+ 2 mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba,+ atapereka malangizo kudzera mwa mzimu woyera kwa atumwi amene iye anawasankha.+ 3 Ndiponso, mwa maumboni ambiri otsimikizika, iye anadzionetsa kwa atumwiwo kuti ali moyo pambuyo pa zovuta zimene anakumana nazo.+ Iwo anamuona masiku onse 40, ndipo anali kuwauza za ufumu wa Mulungu.+ 4 Pamene iye anali pa msonkhano limodzi ndi ophunzirawo, anawapatsa malangizo akuti: “Musatuluke mu Yerusalemu,+ koma muyembekezere chimene Atate analonjeza,+ chimene munamva kwa ine. 5 Chifukwa Yohane anabatizadi ndi madzi, koma pasanathe masiku ambiri mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.”+
6 Tsopano atasonkhana pamodzi, anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu+ kwa Isiraeli pa nthawi ino?” 7 Iye anawayankha kuti: “Si kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo+ zimene Atate waziika pansi pa ulamuliro wake.+ 8 Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.+ Pamenepo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”+ 9 Atatsiriza kunena zimenezi, Mulungu anamunyamula kupita m’mlengalenga iwo akuonerera,+ ndipo mtambo unamuphimba moti sanathenso kumuona.+ 10 Mmene iwo anali kuyang’anitsitsa kuthambo pamene iye anali kukwera kumwamba,+ panaonekera amuna awiri ovala zoyera+ ataimirira pambali pawo. 11 Amunawo anawafunsa kuti: “Amuna inu a ku Galileya, n’chifukwa chiyani muli chilili choncho kuyang’ana kuthambo? Yesu ameneyu, amene watengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati panu, adzabwera m’njira yofanana+ ndi mmene mwamuonera akukwera kuthambo.”
12 Pamenepo anabwerera+ ku Yerusalemu, kuchokera kuphiri lotchedwa phiri la Maolivi. Phiri limeneli lili pafupi ndi Yerusalemu, pa mtunda wa ulendo wa tsiku la sabata.*+ 13 Atafika mumzindawo anakwera m’chipinda cham’mwamba,+ mmene anali kukhala. Mmenemo munali Petulo, Yohane, Yakobo, Andireya, Filipo, Tomasi, Batolomeyo, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Simoni wachangu uja komanso Yudasi mwana wa Yakobo.+ 14 Mogwirizana, onsewa analimbikira kupemphera,+ pamodzi ndi amayi ena+ komanso Mariya mayi a Yesu, limodzinso ndi abale ake a Yesu.+
15 Tsopano m’masiku amenewa, Petulo anaimirira pakati pa abalewo (gulu lonselo linali la anthu pafupifupi 120) n’kunena kuti: 16 “Amuna inu, abale, kudzera pakamwa pa Davide, mzimu woyera+ unaneneratu lemba lokhudza Yudasi,+ amene anatsogolera anthu okagwira Yesu.+ Kunali kofunikira kuti lembalo likwaniritsidwe+ 17 chifukwa anali mmodzi wa ife,+ ndipo anali kutumikira nafe limodzi.+ 18 (Chotero munthu ameneyu, anagula+ munda ndi malipiro a ntchito zosalungama.+ Anagwa chamutu+ n’kuphulika mimba, moti phokoso la kuphulikako linamveka, ndipo matumbo ake onse anakhuthuka. 19 Izi zinadziwika kwa anthu onse okhala mu Yerusalemu, moti munda umenewo anali kuutchula m’chilankhulo chawo kuti A·kelʹda·ma, kutanthauza kuti Munda wa Magazi.) 20 M’buku la Masalimo analembamo kuti, ‘Malo ake okhala asanduke bwinja, ndipo pasapezeke aliyense wokhalamo,’+ komanso kuti, ‘Udindo wake monga woyang’anira utengedwe ndi munthu wina.’+ 21 Choncho n’kofunikira kuti pamalo pake palowe mmodzi mwa amuna amene akhala akusonkhana nafe nthawi zonse pamene Ambuye Yesu anali kuchita zinthu zosiyanasiyana pakati pathu.+ 22 Wotenga malo amenewa akhale munthu amene wakhala akusonkhana nafe kuyambira pamene Yesu anabatizidwa+ ndi Yohane, kudzafika tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati pathu.+ Mmodzi wa amuna amenewa, akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.”+
23 Choncho anaimika awiri, Yosefe wotchedwa Barasaba, amene amadziwikanso kuti Yusito, ndi Matiya. 24 Ndipo anapemphera kuti: “Ambuye wathu Yehova, inu amene mumadziwa mitima ya anthu onse,+ tisonyezeni amene inu mwamusankha mwa amuna awiriwa, 25 kuti atenge malo a utumiki uwu ndi utumwi,+ amene Yudasi anawasiya ndi kuyenda njira zake.” 26 Atatero anachita maere+ pa iwo, ndipo maerewo anagwera Matiya. Choncho iye anamuphatikiza pa atumwi 11+ aja.
2 Tsopano pa tsiku la chikondwerero cha Pentekosite,+ onse anali atasonkhana pamalo amodzi. 2 Mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo unadzaza m’nyumba yonse imene iwo anakhalamo.+ 3 Pamenepo anaona malawi amoto ooneka ngati malilime,+ ndipo anagawanika ndi kukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi. 4 Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana,+ monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.
5 Pa nthawiyo mu Yerusalemu munali kukhala Ayuda ena,+ anthu oopa Mulungu,+ ochokera mu mtundu uliwonse mwa mitundu ya pansi pa thambo. 6 Choncho mkokomo umenewu utamveka, panasonkhana khamu la anthu ambiri. Iwo anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense wa iwo anawamva akulankhula m’chinenero chake. 7 Ndithudi, izi zinawadabwitsa kwambiri moti anayamba kufunsa mothedwa nzeru kuti: “Taonani anthuni, kodi onse akulankhulawa si Agalileya?+ 8 Nanga zikutheka bwanji kuti aliyense wa ife azimva chinenero chimene anabadwa nacho? 9 Pakati pathu pali Apati, Amedi,+ ndi Aelamu.+ Palinso anthu ochokera ku Mesopotamiya, ku Yudeya,+ ku Kapadokiya,+ ku Ponto+ ndi kuchigawo cha Asia.+ 10 Pali anthu ochokera ku Fulugiya,+ ku Pamfuliya,+ ku Iguputo ndi kumadera a Libiya amene ali kufupi ndi Kurene. Palinso alendo ochokera ku Roma, amene ndi Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda,+ 11 komanso Akerete+ ndi Aluya.+ Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu m’zinenero zathu.” 12 Inde, onse anadabwa kwambiri ndi kuthedwa nzeru, n’kumafunsana kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?” 13 Koma ena anali kuwaseka n’kumanena kuti: “Aledzera vinyo watsopano amenewa.”+
14 Koma Petulo anaimirira pamodzi ndi atumwi 11 aja.+ Iye analankhula nawo mokweza mawu kuti: “Anthu inu a m’Yudeya ndi inu nonse okhala m’Yerusalemu,+ dziwani ndi kutchera khutu ku zimene ndikufuna kukuuzani pano. 15 Sikuti anthu awa aledzera+ ngati mmene inu mukuganizira ayi, chifukwa nthawi panopa ndi 9 koloko m’mawa.* 16 Koma zimene zikuchitikazi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti: 17 ‘“Ndipo m’masiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga+ pa anthu osiyanasiyana, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera. Anyamata anu adzaona masomphenya, ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+ 18 Ndidzatsanuliranso mbali ya mzimu wanga ngakhale pa akapolo anga aamuna ndi aakazi m’masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.+ 19 Ndidzachita zodabwitsa kuthambo ndi zizindikiro padziko lapansi. Ndidzachititsa kuti pakhale magazi, moto ndi mtambo wautsi.+ 20 Dzuwa+ lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndi laulemerero la Yehova* lisanafike.+ 21 Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”’+
22 “Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu Mnazareti,+ ndi munthu amene Mulungu anamuonetsera poyera kwa inu. Anatero mwa ntchito zamphamvu,+ mwa zodabwitsa komanso mwa zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ monga mmene inunso mukudziwira. 23 Munthu ameneyu, monga woperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu ndi kudziwiratu kwake zam’tsogolo,+ ndi amene inu munamukhomerera pamtengo ndi kumupha kudzera mwa anthu osamvera malamulo.+ 24 Koma Mulungu anamuukitsa+ kwa akufa mwa kumasula zopweteka za imfa,+ chifukwa zinali zosatheka kuti imfa ipitirize kumugwira mwamphamvu.+ 25 Ponena za iyeyu, pajatu Davide anati, ‘Ndinali kuona Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka ngakhale pang’ono.+ 26 Pa chifukwa chimenechi mtima wanga unakondwera ndipo ndinalankhula mosangalala kwambiri. Komanso, ine ndidzakhala ndi chiyembekezo,+ 27 chifukwa simudzasiya moyo wanga m’Manda,* ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.+ 28 Mwandidziwitsa njira za moyo, ndipo chifukwa cha nkhope yanu ndidzakhala ndi chimwemwe chosefukira.’+
29 “Amuna inu, abale anga, ndilankhula ndithu mwaufulu za kholo lathu Davide. Iye anamwalira+ ndi kuikidwa m’manda, ndipo manda ake tili nawo mpaka lero. 30 Iye anali mneneri, ndipo anali kudziwa kuti Mulungu anam’lonjeza mwa lumbiro, kuti pampando wake wachifumu adzakhazikapo mmodzi mwa zipatso za m’chiuno mwake.+ 31 Choncho pokhala mneneri, iye anaoneratu zapatsogolo ndi kuneneratu za kuuka kwa Khristu. Ananeneratu kuti iye sanasiyidwe m’Manda, komanso kuti thupi lake silinavunde.+ 32 Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za choonadi chimenecho.+ 33 Iye anakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watitsanulira mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu. 34 Ndipotu Davide sanakwere kumwamba,+ koma iye mwini anati, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja+ 35 kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”’+ 36 Choncho nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu, kuti Yesu ameneyu, amene inu munam’pachika,+ Mulungu anamuika kukhala Ambuye+ ndi Khristu.”
37 Tsopano iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima,+ ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Amuna inu, abale athu, tichite chiyani pamenepa?”+ 38 Petulo anawayankha kuti: “Lapani,+ ndipo aliyense wa inu abatizidwe+ m’dzina+ la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe.+ Mukatero mudzalandira mphatso yaulere+ ya mzimu woyera. 39 Pakuti lonjezoli+ laperekedwa kwa inu, kwa ana anu ndi kwa onse akutali,+ onse amene Yehova Mulungu wathu angawasankhe.”+ 40 Ndipo ndi mawu enanso ambiri, Petulo anachitira umboni mokwanira. Komanso sanaleke kuwadandaulira kuti: “Dzipulumutseni ku m’badwo wopotoka maganizo uno.”+ 41 Choncho amene analandira mawu akewo ndi mtima wonse anabatizidwa,+ moti tsiku limenelo chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezeka ndi anthu pafupifupi 3,000.+ 42 Chotero iwo anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa. Iwo anali kugawana zinthu,+ kudya chakudya+ komanso kupemphera.+
43 Pamenepo anthu onse anayamba kuchita mantha, ndipo atumwiwo anayamba kuchita zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri.+ 44 Onse amene anakhala okhulupirira anasonkhana pamodzi ndipo zinthu zonse zimene anali nazo zinali za onse.+ 45 Anali kugulitsa malo awo ndi zina zimene anali nazo,+ n’kugawa kwa onse zimene apeza, aliyense malinga ndi kusowa kwake.+ 46 Tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi mogwirizana.+ Analinso kuyenderana m’nyumba zawo ndi kudyera limodzi chakudya mosangalala+ ndiponso ndi mtima wofunitsitsa kugawana zinthu. 47 Anali kutamanda Mulungu ndipo anthu onse anali kuwakonda.+ Komanso tsiku ndi tsiku, Yehova anapitiriza kuwawonjezera+ anthu amene anali kuwapulumutsa.+
3 Tsopano Petulo ndi Yohane anali kukalowa m’kachisi pa ola la kupemphera, 3 koloko masana.*+ 2 Ndiyeno tsiku ndi tsiku anthu anali kunyamula mwamuna wina amene anabadwa ali wolumala.+ Iwo anali kukhazika wolumalayo pafupi ndi khomo la kachisi lotchedwa Chipata Chokongola,+ kuti azipempha mphatso zachifundo kwa olowa m’kachisimo.+ 3 Munthuyu ataona Petulo ndi Yohane ali pafupi kulowa m’kachisimo anayamba kupempha kuti amupatse mphatso zachifundo.+ 4 Koma Petulo, pamodzi ndi Yohane, anamuyang’anitsitsa+ n’kunena kuti: “Tiyang’ane.” 5 Iye anawayang’anitsitsa, akuyembekeza kuti amupatsa kanthu. 6 Koma Petulo anati: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho:+ M’dzina la Yesu Khristu Mnazareti,+ yenda!”+ 7 Atatero anamugwira dzanja lake lamanja+ ndi kumuimiritsa. Nthawi yomweyo kunsi kwa mapazi ake komanso mafupa ake a akakolo zinalimba.+ 8 Pamenepo anadumpha n’kuimirira,+ ndi kuyamba kuyenda. Ndipo analowa nawo limodzi m’kachisimo,+ akuyenda, kudumphadumpha ndi kutamanda Mulungu. 9 Anthu onse+ anamuona akuyenda ndi kutamanda Mulungu. 10 Kenako anayamba kumuzindikira kuti ndi mwamuna amene anali kukhala pa Chipata Chokongola+ cha kachisi n’kumapempha mphatso zachifundo. Ndipo iwo anadabwa ndi kuzizwa kwambiri+ ndi zimene zinam’chitikirazo.
11 Tsopano munthu uja atakangamira Petulo ndi Yohane osawasiya, anthu onse pamodzi anakhamukira kwa iwo pamalo otchedwa khonde la zipilala la Solomo,+ ali odabwa kwambiri. 12 Petulo ataona zimenezi, anauza anthuwo kuti: “Aisiraeli inu, n’chifukwa chiyani mukudabwa nazo zimenezi? N’chifukwa chiyani mukutiyang’anitsitsa ngati kuti tamuyendetsa mwa mphamvu zathu, kapena chifukwa cha kudzipereka kwathu kwa Mulungu?+ 13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo,+ Mulungu wa makolo athu, ndi amene walemekeza+ Mtumiki+ wake Yesu, amene inu munamupereka+ ndi kumukana pamaso pa Pilato, Pilatoyo akufuna kumumasula.+ 14 Inde, inu munakana woyera ndi wolungamayo,+ ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wina, munthu wopha anthu.+ 15 Chotero munapha Mtumiki Wamkulu wa moyo,+ koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, ndipo ife ndife mboni za choonadi chimenechi.+ 16 Choncho mwa chikhulupiriro chathu m’dzina lake, dzina lakelo lalimbitsa mwamunayu amene mukumuona ndi kumudziwa. Ndipo chikhulupiriro chimene ife tili nacho chifukwa cha iye chamuchiritsiratu, monga mmene nonsenu mukuonera. 17 Ndipo tsopano abale, ndikudziwa kuti munachita zinthu mosadziwa,+ ngati mmenenso olamulira+ anu anachitira. 18 Koma mwanjira imeneyi Mulungu wakwaniritsa zimene analengezeratu kudzera mwa aneneri onse, kuti Khristu wake adzavutika.+
19 “Chotero lapani+ ndi kutembenuka+ kuti machimo anu afafanizidwe,+ ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa+ zibwere kuchokera kwa Yehova. 20 Komanso kuti atumize Yesu, amene ndiye Khristu woikidwa chifukwa cha inu. 21 Ameneyu kumwamba kuyenera kumusunga+ mpaka nthawi za kubwezeretsa+ zinthu zonse, kumene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera+ akale. 22 Ndipotu Mose ananena kuti, ‘Yehova Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu.+ Mudzamumvere pa zinthu zonse zimene adzakuuzeni.+ 23 Ndithudi, munthu aliyense amene sadzamvera Mneneri ameneyo Mulungu adzamuwononga ndi kumuchotsa pakati pa anthu ake.’+ 24 Ndipo aneneri onse, kuyambira pa Samueli mpaka aneneri onse amene anabwera m’mbuyo mwake, onse amene analosera, ananena mosapita m’mbali za masiku amenewa.+ 25 Inu ndinu ana+ a aneneri ndi a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo anu akale. Iye anauza Abulahamu kuti, ‘Kudzera mwa mbewu yako mabanja onse a padziko lapansi adzadalitsidwa.’+ 26 Mulungu atasankha Mtumiki wake, choyamba anamutumiza kwa inu,+ kuti adzakudalitseni mwa kubweza aliyense wa inu kuti musiye ntchito zanu zoipa.”
4 Pamene Petulo ndi Yohane anali kulankhula ndi anthuwo, ansembe aakulu, woyang’anira kachisi+ ndi Asaduki+ anafika kwa iwo. 2 Iwo anali okwiya chifukwa atumwiwo anali kuphunzitsa anthu ndi kulalikira mosapita m’mbali za kuuka kwa akufa pogwiritsa ntchito chitsanzo cha Yesu.+ 3 Choncho anawagwira ndi kuwasunga m’ndende mpaka tsiku lotsatira,+ chifukwa anali kale madzulo. 4 Koma anthu ambiri amene anamvetsera mawu awo anakhulupirira,+ ndipo chiwerengero cha amuna chinakwana pafupifupi 5,000.+
5 Tsiku lotsatira, olamulira ndi akulu ndiponso alembi anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu.+ 6 (Pamenepo panalinso Anasi+ wansembe wamkulu, Kayafa,+ Yohane, Alekizanda, ndi achibale ambiri a wansembe wamkuluyo.) 7 Ndiyeno anaimika atumwiwo pakati pawo n’kuyamba kuwafunsa kuti: “Kodi mwachita zimenezi ndi ulamuliro uti kapena m’dzina la ndani?”+ 8 Pamenepo Petulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera,+ anawayankha kuti:
“Olamulira anthu ndiponso akulu inu, 9 ngati pa ntchito yabwino imene tachita kwa wodwalayu,+ lero tikufunsidwa kuti tamuchiritsa m’dzina la ndani, 10 dziwani nonsenu ndi Aisiraeli onse, kuti m’dzina la Yesu Khristu Mnazareti+ uja, amene inu munamupachika pamtengo,+ koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa,+ kudzera mwa iyeyo, munthu uyu waimirira pamaso panu atachira bwinobwino. 11 Yesu ameneyu ndiye ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’+ 12 Ndiponso chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina+ pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”+
13 Tsopano ataona mmene Petulo ndi Yohane anali kulankhulira molimba mtima, komanso atazindikira kuti anali anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba,+ anadabwa kwambiri. Ndipo anayamba kuwazindikira kuti anali kuyenda ndi Yesu.+ 14 Ndiyeno poona munthu wochiritsidwa uja ataimirira nawo limodzi,+ analibe chonena kuti awatsutse.+ 15 Choncho anawalamula kuti atuluke muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda,* ndipo anayamba kufunsana, 16 kuti: “Tichite nawo chiyani amuna amenewa?+ Chifukwa kunena zoona, iwo achitadi chizindikiro chachikulu, chimene chaonekera kwa onse okhala mu Yerusalemu.+ Ndipo ife sitingatsutse zimenezi. 17 Komabe, kuti nkhaniyi isapitirire kufalikira kwa anthu ena, tiyeni tiwaopseze kuti asalankhulenso m’dzina limeneli kwa munthu wina aliyense.”+
18 Atatero anawaitana ndi kuwalamula kuti asalankhulenso kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu kwina kulikonse. 19 Koma poyankha, Petulo ndi Yohane anawauza kuti: “Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. 20 Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”+ 21 Choncho atawonjezera kuwaopseza, anawamasula, pakuti sanapeze chifukwa chilichonse chowapatsira chilango. Komanso anaopa anthu,+ pakuti onse anali kutamanda Mulungu chifukwa cha zimene zinachitikazo. 22 Ndipotu chizindikiro cha machiritsochi chinachitika kwa munthu amene anali ndi zaka zopitirira 40.
23 Atawamasula anapita kwa okhulupirira anzawo,+ ndipo anawafotokozera zonse zimene ansembe aakulu, ndi akulu anawauza. 24 Atamva zimenezi, onse pamodzi anafuula kwa Mulungu+ mokweza mawu kuti:
“Ambuye Wamkulu Koposa,+ Inu ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.+ 25 Ndinu amene mwa mzimu woyera, munanena kudzera pakamwa pa kholo lathu Davide,+ mtumiki wanu kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe, ndiponso n’chifukwa chiyani mitundu ya anthu ikusinkhasinkha zinthu zopanda pake?+ 26 Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo, ndipo olamulira asonkhana pamodzi mogwirizana, kuti alimbane ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.’+ 27 Zimenezi zinachitikadi pamene Herode,* Pontiyo Pilato,+ pamodzi ndi anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzinda uno ndi kuukira Yesu, mtumiki wanu woyera,+ amene inu munamudzoza.+ 28 Iwo anasonkhana pamodzi kuti achite zimene inu munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa chakuti zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+ 29 Koma tsopano Yehova, imvani mmene akutiopsezera,+ ndipo lolani kuti akapolo anu apitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.+ 30 Pitirizani kutambasula dzanja lanu ndi kupereka machiritso, komanso kuti zizindikiro ndi zodabwitsa+ zipitirize kuchitika m’dzina+ la Yesu, mtumiki wanu woyera.”+
31 Atatha kupembedzera, malo amene anasonkhanawo anagwedezeka.+ Pamenepo aliyense wa iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera,+ ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.+
32 Ndipo onse amene anakhulupirira anakhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ Panalibe ngakhale mmodzi wonena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.+ 33 Komanso, atumwiwo anapitiriza kuchitira umboni mwamphamvu kwambiri za kuuka kwa Ambuye Yesu.+ Ndipo kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kunali pa onsewo. 34 Ndithudi, panalibe ngakhale mmodzi wosowa kanthu pakati pawo.+ Onse amene anali ndi minda kapena nyumba, anali kuzigulitsa ndi kubweretsa ndalamazo, 35 kudzazipereka kwa atumwi.+ Ndiyeno ndalamazo anali kuzigawa+ kwa aliyense malinga ndi zosowa zake. 36 Choncho Yosefe, amene atumwiwo anamutchanso Baranaba,+ dzina limene polimasulira limatanthauza, Mwana wa Chitonthozo, amene anali Mlevi, komanso mbadwa ya ku Kupuro, 37 anali ndi munda. Iye anagulitsa mundawo ndi kubweretsa ndalamazo kudzazipereka kwa atumwi.+
5 Tsopano munthu wina, dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsa munda wawo. 2 Koma mobisa iye anapatula zina mwa ndalamazo n’kusunga, mkazi wakenso anadziwa zimenezo. Ndiyeno anabweretsa zotsalazo n’kudzazipereka kwa atumwi.+ 3 Koma Petulo anati: “Hananiya, n’chifukwa chiyani Satana+ wakulimbitsa mtima choncho kuti uyese kunamiza+ mzimu woyera+ ndi kubisa zina mwa ndalama za mtengo wa mundawo? 4 Kodi mundawo sunali m’manja mwako usanaugulitse? Ndipo utaugulitsa, kodi ndalamazo sukanatha kuchita nazo mmene ukanafunira? N’chifukwa chiyani mumtima mwako unaganiza zochita zinthu zimenezi? Pamenepa sikuti wanamiza+ anthu ayi, koma Mulungu.”+ 5 Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi ndi kumwalira.+ Ndipo onse amene anamva zimenezi anagwidwa ndi mantha aakulu.+ 6 Pamenepo anyamata anabwera ndi kumukulunga pansalu.+ Kenako anatuluka naye ndi kukamuika m’manda.
7 Tsopano patapita maola pafupifupi atatu mkazi wake analowa, osadziwa chimene chachitika. 8 Ndiyeno Petulo anamufunsa kuti: “Tandiuza, kodi ndalama zonse zimene awirinu mwapeza mutagulitsa munda wanu ndi izi?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndi zomwezo.” 9 Pamenepo Petulo anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani awirinu munagwirizana kuti muyese+ mzimu wa Yehova? Taona! Anthu amene anapita kukaika mwamuna wako m’manda ali pakhomo. Iwenso akunyamula ndi kutuluka nawe.” 10 Nthawi yomweyo anagwa pansi pamapazi a Petulo n’kumwalira.+ Pamene anyamata aja amalowa anam’peza atafa kale. Choncho anamunyamula ndi kutuluka naye kukamuika m’manda pafupi ndi mwamuna wake. 11 Zitatero mpingo wonse ndi onse amene anamva zimenezi anagwidwa ndi mantha aakulu.
12 Choncho atumwiwo anapitiriza kuchita zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri pakati pa anthu.+ Ndipo okhulupirira onse mogwirizana anali kusonkhana m’khonde la zipilala la Solomo.+ 13 Ndithudi, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa enawo amene analimba mtima kuphatikana ndi ophunzirawo,+ koma anthu anali kuwatamanda.+ 14 Komanso okhulupirira Ambuye anapitiriza kuwonjezeka, chifukwa amuna ndi akazi ambirimbiri anakhala ophunzira.+ 15 Mwakuti anthuwo anabweretsa odwala m’misewu atawagoneka patimabedi ndi pamachira. Anachita izi kuti pamene Petulo akudutsa, chithunzithunzi chake chokhacho chigwere ena mwa iwo.+ 16 Ndiponso anthu ambirimbiri ochokera m’mizinda yozungulira Yerusalemu anali kukhamukira kumeneko, atanyamula anthu odwala komanso amene mizimu yonyansa inali kuwazunza. Ndipo onsewo anali kuchiritsidwa.
17 Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, gulu la mpatuko la Asaduki la pa nthawiyo, anachita nsanje.+ Ndipo ananyamuka 18 ndi kugwira atumwiwo n’kuwatsekera m’ndende.+ 19 Koma usiku, mngelo wa Yehova+ anatsegula zitseko za ndendeyo+ ndi kuwatulutsa, ndipo anawauza kuti: 20 “Pitani, ndipo mukaimirire m’kachisi ndi kupitiriza kuuza anthu zoyenera kuchita kuti adzapeze moyo umene ukubwerawo.”+ 21 Atamva zimenezi, analowa m’kachisi m’mawa kwambiri ndi kuyamba kuphunzitsa.
Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye atafika, anasonkhanitsa pamodzi Khoti Lalikulu la Ayuda ndi bungwe lonse la akulu a ana a Isiraeli.+ Pamenepo anatumiza alonda kundende kuja kuti akatenge atumwiwo ndi kubwera nawo. 22 Koma pamene alonda aja anafika kumeneko sanawapeze m’ndendemo. Choncho anabwerera ndi kukanena zimenezi. 23 Iwo anati: “Ife tapeza ndende ili yokhoma ndi yotetezedwa bwino, alonda ali chilili m’makomo. Koma titatsegula sitinapezemo aliyense.” 24 Tsopano woyang’anira kachisi ndi ansembe aakulu atamva mawu amenewa, anathedwa nzeru ndi zimenezi posadziwa kuti chichitike n’chiyani.+ 25 Koma panafika munthu wina amene anawauza kuti: “Tamverani! Amuna munawatsekera m’ndende aja ali m’kachisi, aimirira mmenemo ndipo akuphunzitsa anthu.”+ 26 Pamenepo woyang’anira kachisi uja ananyamuka ndi alonda ake n’kukawatenga. Koma sanawatenge mwachiwawa, poopa+ kuti anthu awaponya miyala.
27 Choncho anabwera nawo ndi kuwaimiritsa m’holo ya Khoti Lalikulu la Ayuda. Ndipo mkulu wa ansembe ananena 28 kuti: “Tinakulamulani mwamphamvu+ kuti musadzaphunzitsenso m’dzina limeneli, koma taonani tsopano! Mwadzaza Yerusalemu yense ndi chiphunzitso chanuchi,+ ndipo mwatsimikiza mtima ndithu kuti mubweretse magazi+ a munthu ameneyu pa ife.” 29 Poyankha Petulo ndi atumwi enawo ananena kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.+ 30 Mulungu wa makolo athu anaukitsa+ Yesu, amene inu munamupha mwa kumupachika pamtengo.+ 31 Ameneyo Mulungu anamukweza kudzanja lake lamanja+ monga Mtumiki Wamkulu+ ndi Mpulumutsi.+ Anachita zimenezi kuti Aisiraeli alape+ ndi kuti machimo awo akhululukidwe.+ 32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zimenezi,+ chimodzimodzinso mzimu woyera,+ umene Mulungu wapereka kwa anthu omumvera monga wolamulira.”
33 Atamva zimenezi, anakwiya kwambiri moti anafuna kungowapha basi.+ 34 Koma mwamuna wina anaimirira pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Iyeyu anali Mfarisi wotchedwa Gamaliyeli,+ mphunzitsi wa Chilamulo wolemekezedwa ndi anthu onse. Ndiyeno analamula kuti anthuwo awatulutse kwa kanthawi.+ 35 Pamenepo anawauza kuti: “Amuna inu Aisiraeli,+ musamale ndi zimene mukufuna kuwachita anthu awa. 36 Chifukwa m’masiku am’mbuyomu, kunali Teuda amene anadzitchukitsa kwambiri+ ndipo amuna pafupifupi 400 analowa m’gulu lake.+ Koma anaphedwa, ndipo onse amene anali kumutsatira anabalalitsidwa osaonekanso. 37 Kenako kunali Yudasi Mgalileya m’masiku a kalembera.+ Iyeyu anakopa anthu ndipo anamutsatira. Koma munthu ameneyunso anafa, ndipo onse amene anali kumutsatira anabalalikabalalika. 38 Choncho mmene zinthu zilili panopa, ndikukuuzani kuti, Alekeni amuna amenewa musalimbane nawo. Chifukwa ngati zolinga zawo kapena ntchito iyi ikuchokera kwa anthu, sipita patali.+ 39 Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu,+ simungathe kuwaletsa.+ Mukaumirira mukhoza kupezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”+ 40 Pamenepo iwo anamvera mawu ake, ndipo anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno anangowakwapula+ ndi kuwalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu,+ kenako anawamasula.
41 Choncho atumwiwo anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala+ chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.+ 42 Ndipo tsiku ndi tsiku m’kachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba,+ anapitiriza mwakhama kuphunzitsa+ ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.+
6 Tsopano m’masiku amenewo, pamene ophunzirawo anali kuchulukirachulukira, Ayuda olankhula Chigiriki+ anayamba kudandaula za Ayuda olankhula Chiheberi. Chifukwa chakuti akazi amasiye achigiriki anali kunyalanyazidwa pa kagawidwe ka chakudya cha tsiku ndi tsiku.+ 2 Chotero atumwi 12 aja anaitana khamu la ophunzira ndi kunena kuti: “N’kosayenera kuti ife tisiye ntchito yophunzitsa mawu a Mulungu n’kuyamba kugawa chakudya.+ 3 Chotero abale, fufuzani+ pakati panu amuna 7 a mbiri yabwino, amene ali ndi mzimu komanso nzeru zochuluka,+ kuti ife tiwaike kukhala oyang’anira ntchito yofunikayi. 4 Koma ife tidzipereka ndithu pa kupemphera ndi pa utumiki wokhudza mawu a Mulungu.”+ 5 Mawu amenewa anasangalatsa khamu lonselo, mwakuti anasankha Sitefano, mwamuna wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndi mzimu woyera.+ Anasankhanso Filipo,+ Purokoro, Nikanora, Timoni, Paremena ndi Nikolao wa ku Antiokeya amene anali wotembenukira ku Chiyuda. 6 Ndiyeno anawaimiritsa pamaso pa atumwiwo, ndipo atapemphera, atumwiwo anaika manja+ awo pa iwo.
7 Pamenepo mawu a Mulungu anapitiriza kufalikira ponseponse.+ Chiwerengero cha ophunzira chinali kuwonjezeka kwambiri mu Yerusalemu.+ Ndipo ansembe ambirimbiri+ anakhala okhulupirira.+
8 Tsopano Sitefano, anali wodzazidwa ndi chisomo komanso mphamvu, ndipo anali kuchita zodabwitsa ndi zizindikiro zazikulu+ pakati pa anthu. 9 Ndiyeno panafika amuna ena a gulu lotchedwa Sunagoge wa Omasulidwa, ndi ena a ku Kurene, a ku Alekizandiriya,+ komanso ena ochokera ku Kilikiya+ ndi ku Asia, kudzatsutsana ndi Sitefano. 10 Koma iwo sanathe kulimbana ndi nzeru+ zimene anasonyeza komanso mzimu woyera umene unali kumutsogolera pamene anali kulankhula.+ 11 Kenako mwamseri ananyengerera amuna ena kuti anene kuti:+ “Tamumva ife ameneyu akulankhula mawu onyoza+ Mose ndi Mulungu.” 12 Pamenepo ananyanyula mitima ya anthu, akulu ndi alembi. Ndiyeno anamufikira mwadzidzidzi n’kumugwira, ndipo anapita naye ku Khoti Lalikulu la Ayuda.+ 13 Kumeneko anabweretsa mboni zonama,+ zimene zinati: “Munthu uyu sakuleka kulankhula mawu onyoza malo oyera ano ndi Chilamulo.+ 14 Mwachitsanzo, ife tinamumva iyeyu akunena kuti Yesu Mnazareti uja adzawononga malo oyera ano ndi kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”
15 Ndipo pamene onse amene anakhala m’bwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda anamuyang’anitsitsa,+ anaona kuti nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo.+
7 Koma mkulu wa ansembe anati: “Kodi zimenezi n’zoona?” 2 Sitefano anati: “Amuna inu, abale anga ndi abambo anga, mvetserani! Mulungu waulemerero+ anaonekera kwa kholo lathu Abulahamu pamene anali ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harana.+ 3 Ndipo anamuuza kuti, ‘Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako. Tiye ukalowe m’dziko limene ine ndidzakusonyeza.’+ 4 Pamenepo anasamuka m’dziko la Akasidi ndi kukakhala ku Harana. Kumeneko, pambuyo pa imfa ya bambo ake,+ Mulungu anamuuza kuti asamukire m’dziko lino limene inu mukukhala tsopano.+ 5 Komatu sanam’patse cholowa chilichonse mmenemu ayi, ngakhale kadera kochepetsetsa.+ Koma anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikoli monga cholowa chake,+ ndi cha mbewu yake,+ ngakhale kuti pa nthawiyo n’kuti alibe mwana.+ 6 Ndipo Mulungu ananenanso kuti mbewu yake idzakhala alendo+ m’dziko lachilendo,+ ndipo anthu adzawasandutsa akapolo ndi kuwasautsa kwa zaka 400.+ 7 Mulungu anati, ‘Ndidzaweruza mtundu umene adzautumikire monga akapolo,+ pambuyo pake adzatuluka ndi kudzanditumikira m’malo ano.’+
8 “Anamupatsanso pangano la mdulidwe.+ Chotero anabereka Isaki+ ndi kuchita mdulidwe wake tsiku la 8.+ Isaki naye anabereka Yakobo, Yakobo anabereka mitu ya mabanja 12 ija.+ 9 Mitu ya mabanja ija inachitira nsanje+ Yosefe ndi kumugulitsa ku Iguputo.+ Koma Mulungu anali naye,+ 10 ndipo anamulanditsa m’masautso ake onse. Anamupatsanso chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya Iguputo. Ndipo anamuika kuti ayang’anire Iguputo ndi nyumba yonse ya Farao.+ 11 Tsopano munagwa njala yaikulu mu Iguputo ndi mu Kanani monse, inde chisautso chachikulu. Ndipo makolo athuwo sanali kupeza chakudya.+ 12 Koma Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli chakudya,+ ndipo anatuma makolo athu aja kwa nthawi yoyamba.+ 13 Pa ulendo wachiwiri Yosefe anadziulula kwa abale ake,+ ndipo Farao anadziwa za achibale ake onse a Yosefe ndi makolo ake.+ 14 Chotero Yosefe anatumiza anthu ku Kanani kukatenga bambo ake Yakobo ndi achibale ake.+ Onse pamodzi analipo anthu 75.+ 15 Yakobo anapita ku Iguputo+ kumene iye ndi makolo athu+ aja anamwalirira.+ 16 Kenako mafupa awo anawatengera ku Sekemu,+ kumene anakawaika m’manda.+ Anawaika m’manda amene Abulahamu anagula ndi ndalama zasiliva kwa ana a Hamori mu Sekemu.+
17 “Nthawi itayandikira, yakuti lonjezo likwaniritsidwe limene Mulungu anapereka kwa Abulahamu, mtundu wa anthu unakula ndi kuwonjezeka mu Iguputo.+ 18 Kenako, mfumu ina imene sinali kudziwa za Yosefe inayamba kulamulira mu Iguputo.+ 19 Mfumu imeneyi inagwiritsa ntchito ulamuliro wake molakwika pofuna kuzunza anthu a fuko lathu,+ ndipo mwankhanza inachititsa makolo athuwo kutaya makanda awo, kuti asakhale ndi moyo.+ 20 Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa,+ ndipo anali wokongola kwambiri, ngakhalenso pamaso pa Mulungu.+ Mose analeredwa m’nyumba ya bambo ake kwa miyezi itatu. 21 Koma pamene anamusiya yekha, mwana wamkazi wa Farao anamutola ndi kumulera ngati mwana wake.+ 22 Chotero Mose anaphunzira nzeru+ zonse za Aiguputo. Ndipo anali wamphamvu m’mawu+ ndi m’zochita zake.
23 “Tsopano pamene anakwanitsa zaka 40 zakubadwa, anaganiza zokayendera abale ake, ana a Isiraeli.+ 24 Ataona winawake akuzunzidwa, anamutchinjiriza ndi kupha Mwiguputo wozunzayo pobwezera m’malo mwa wozunzidwa uja.+ 25 Mose anali kuganiza kuti abale akewo azindikira kuti Mulungu akuwapatsa chipulumutso kudzera m’dzanja lake,+ koma iwo sanaizindikire mfundo imeneyi. 26 Tsiku lotsatira anaonekera kwa iwo pamene anali kumenyana, ndipo anayesa kuwayanjanitsa+ mwa kunena kuti, ‘Amuna inu, ndinu pachibale. N’chifukwa chiyani mukuzunzana chonchi?’+ 27 Koma amene anali kuzunza mnzakeyo anamukankha ndi kunena kuti, ‘Iweyo anakuika ndani kuti ukhale wolamulira ndi woweruza wathu?+ 28 Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera Mwiguputo uja dzulo?’+ 29 Atamva mawu amenewa, Mose anathawa ndi kukakhala kuchilendo m’dziko la Midiyani.+ Kumeneko anabereka ana aamuna awiri.+
30 “Patapita zaka 40, mngelo anaonekera kwa iye m’malawi a moto pachitsamba chaminga+ m’chipululu, pafupi ndi phiri la Sinai. 31 Tsopano Mose ataona zimenezi, anadabwa kwambiri.+ Koma pamene anali kuyandikira kuti aonetsetse, panatuluka mawu a Yehova* akuti, 32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako. Ndine Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo.’+ Ponjenjemera ndi mantha, Mose sanathenso kupitiriza kuyang’anitsitsa chitsambacho. 33 Yehova anamuuza kuti, ‘Vula nsapato zako, pakuti malo amene waimawo ndi malo oyera.+ 34 Ine ndaona ndithu mmene anthu anga amene ali ku Iguputo akuwazunzira.+ Ndamva kubuula kwawo+ ndipo ndatsika kudzawalanditsa.+ Tsopano tamvera. Ndikufuna ndikutume ku Iguputo.’+ 35 Mose ameneyo, amene iwo anamukana ndi kunena kuti, ‘Iweyo anakuika ndani kuti ukhale wolamulira ndi woweruza wathu?’+ munthu ameneyo ndi amene Mulungu anamutumiza+ monga wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga chija. 36 Munthu ameneyo anawatsogolera ndi kutuluka nawo,+ atachita zodabwitsa ndi zizindikiro mu Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndi m’chipululu kwa zaka 40.+
37 “Ameneyu ndi Mose amene anauza ana a Isiraeli kuti, ‘Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati pa abale anu.’+ 38 Uyu ndi amene+ anali pakati pa mpingo+ m’chipululu limodzi ndi mngelo+ amene analankhula ndi iyeyu komanso makolo athu paphiri la Sinai. Pamenepo analandira mawu opatulika+ omwe ndi amphamvu kuti awapereke kwa inu. 39 Koma makolo athu akale anakana kumumvera. M’malomwake, anamukankhira kumbali,+ ndipo mumtima mwawo anabwerera ku Iguputo.+ 40 Anauza Aroni kuti, ‘Tipangire milungu ititsogolere. Chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitsogolera potuluka m’dziko la Iguputo.’+ 41 Choncho iwo anapanga mwana wa ng’ombe m’masiku amenewo,+ ndi kubweretsa nsembe kwa fano limenelo. Pamenepo anasangalala ndi ntchito za manja awo.+ 42 Chotero Mulungu anawaleka+ kuti atumikire makamu akumwamba monga mmene malemba amanenera m’buku la aneneri.+ Malembawo amati, ‘Anthu inu a nyumba ya Isiraeli, kodi m’chipululu muja munali kupereka kwa ine nyama zansembe ndi zopereka zina kwa zaka 40?+ 43 Inutu munali kunyamula chihema cha Moloki+ ndi nyenyezi+ ya mulungu Refani, mafano amene munapanga kuti muziwalambira. Chotero ndidzakupitikitsirani+ kutali kupitirira Babulo.’
44 “Makolo athuwo anali ndi chihema cha umboni m’chipululu. Anachipanga potsatira malangizo amene Mulungu anapereka pamene anali kulankhula ndi Mose. Mulungu anauza Mose kuti apange chihemacho molingana ndi chithunzi chimene anachiona.+ 45 Ndipo makolo athu amene anachilandira kwa makolo awo, analowa nacho limodzi ndi Yoswa,+ m’dziko limene linali m’manja mwa anthu a mitundu ina+ amene Mulungu anawapitikitsa pamaso pa makolo athu.+ Chihemacho chinakhala m’dziko limeneli mpaka m’masiku a Davide. 46 Mulungu anakomera mtima+ Davide ndipo iye anapempha mwayi wakuti amange nyumba yokhalamo+ Mulungu wa Yakobo. 47 Koma Solomo ndiye anamangira Mulungu nyumba.+ 48 Ngakhale ndi choncho, Wam’mwambamwamba sakhala m’nyumba zomangidwa ndi manja,+ monga mneneri akunenera kuti, 49 ‘Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu,+ ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.+ Kodi inu mudzandimangira nyumba yotani? akutero Yehova. Kapena malo oti ine ndipumuliremo ali kuti?+ 50 Kodi si dzanja langa limene linapanga zinthu zonsezi?’+
51 “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+ 52 Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Inde, iwo anapha+ amene analengezeratu za kubwera kwa Wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndi kumupha,+ 53 inu amene munalandira Chilamulo kudzera mwa angelo,+ koma osachisunga.”
54 Atamva zimenezi, anakwiya koopsa+ ndipo anayamba kumukukutira+ mano. 55 Koma iye, pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyera, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelero wa Mulungu ndi wa Yesu ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu.+ 56 Ndipo ananena kuti: “Taonani! Ndikuona kumwamba kotseguka,+ ndipo Mwana wa munthu+ waimirira kudzanja lamanja la Mulungu.”+ 57 Iwo atamva zimenezi anafuula mokuwa atatseka m’makutu ndi manja awo,+ ndipo onse pamodzi anathamangira kwa iye. 58 Atamutulutsira kunja kwa mzinda,+ anayamba kumuponya miyala.+ Ndipo mboni+ zinaika malaya awo akunja pafupi ndi mnyamata wina dzina lake Saulo.+ 59 Iwo anapitiriza kumuponya miyala Sitefano, pamene iye anali kuchonderera kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu* wanga.”+ 60 Kenako anagwada pansi ndi kufuula ndi mawu amphamvu kuti: “Yehova, musawaimbe mlandu wa tchimo ili.”+ Atanena zimenezi anagona tulo ta imfa.
8 Ndiyeno Saulo anali kuvomereza za kupha Sitefano.+
Tsiku limenelo, panabuka chizunzo chachikulu+ choukira mpingo umene unali mu Yerusalemu. Onse anabalalikira+ m’zigawo za Yudeya ndi Samariya, kupatulapo atumwi okha. 2 Koma amuna ena oopa Mulungu anatenga Sitefano ndi kukamuika m’manda,+ ndipo anamulira kwambiri.+ 3 Tsopano Saulo anayamba kuzunza mpingo mwankhanza. Anali kulowa m’nyumba ndi nyumba, ndi kukokera panja amuna ndi akazi omwe, n’kukawaponya m’ndende.+
4 Komabe, amene anabalalitsidwa aja anapita m’zigawozo akulengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.+ 5 Koma Filipo anapita kumzinda wa Samariya+ ndi kuyamba kulalikira za Khristu kwa anthu akumeneko. 6 Makamu a anthu anali kutchera khutu ndi mtima umodzi ndi kumvetsera zimene Filipo anali kunena. Iwo anali kumvetsera ndi kuona zizindikiro zimene iye anali kuchita. 7 Kumeneko kunali anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yonyansa,+ ndipo inali kufuula mokweza mawu ndi kutuluka. Ndipo anthu ambiri amene anali akufa ziwalo+ ndi olumala anali kuchiritsidwa. 8 Choncho mumzindawo munali chimwemwe chachikulu.+
9 Tsopano mumzindawo munalinso munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanachitike, iyeyu anali kuchita zamatsenga+ ndi kudabwitsa anthu onse mu Samariya. Anali kudzitamandira kuti anali wopambana.+ 10 Chotero onse, aang’ono ndi aakulu omwe, anali kumumvetsera ndi kunena kuti: “Munthu uyu ndiyedi Mphamvu ya Mulungu, imene tingati ndi Yaikulu.” 11 Chotero anali kumumvetsera chifukwa anawadabwitsa ndi zamatsenga zakezo kwa nthawi yaitali. 12 Koma iwo atakhulupirira Filipo, amene anali kulengeza uthenga wabwino wonena za ufumu wa Mulungu+ ndi za dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.+ 13 Simoni uja nayenso anakhala wokhulupirira. Atabatizidwa, sanali kusiyana ndi Filipo+ kulikonse. Moti anali kudabwa poona zizindikiro ndi ntchito zamphamvu zazikulu zikuchitika.
14 Pamene atumwi ku Yerusalemu anamva kuti Asamariya alandira mawu a Mulungu,+ anawatumizira Petulo ndi Yohane. 15 Iwo anapitadi kumeneko ndipo anawapempherera kuti alandire mzimu woyera.+ 16 Pa nthawiyi n’kuti mzimu woyerawo usanafike pa aliyense wa iwo, koma anali atangobatizidwa chabe m’dzina la Ambuye Yesu.+ 17 Chotero atumwiwo anayamba kuika manja awo pa anthuwo,+ ndipo analandira mzimu woyera.
18 Tsopano Simoni uja ataona kuti atumwiwo, mwa kungoika manja pa anthuwo, mzimu woyera unali kuperekedwa, anafuna kuwapatsa ndalama.+ 19 Iye ananena kuti: “Inenso mundipatseko mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndizimuika manja azilandira mzimu woyera.” 20 Koma Petulo anamuuza kuti: “Siliva wakoyo awonongeke nawe limodzi, chifukwa ukuganiza kuti mphatso yaulere ya Mulungu ungaipeze ndi ndalama.+ 21 Ulibe gawo kapena mbali mu ntchito imeneyi, pakuti mtima wako si wowongoka pamaso pa Mulungu.+ 22 Chotero lapa choipa chakochi, ndipo upemphe kwa Yehova mopembedzera+ kuti ngati n’kotheka, maganizo oipa a mtima wakowo akhululukidwe. 23 Pakuti ndaona kuti ndiwe ndulu yaululu+ ndipo mwa iwe mwadzaza kusalungama.”+ 24 Poyankha Simoni uja anati: “Amuna inu, ndipemphereni chonde kwa Yehova mopembedzera+ kuti zonse mwanenazo zisandigwere.”
25 Choncho atatha kuchitira umboni mokwanira ndi kulankhula mawu a Yehova, anabwerera ku Yerusalemu. Pamene anali kubwerera anali kulengeza uthenga wabwino m’midzi yambiri ya Asamariya.+
26 Koma mngelo wa Yehova+ analankhula kwa Filipo kuti: “Nyamuka ndi kulowera kum’mwera, kumsewu wochokera ku Yerusalemu kupita ku Gaza.” (Umenewu ndi msewu wa m’chipululu.) 27 Choncho, ananyamuka ndi kupita. Kumeneko anakumana ndi nduna+ ya ku Itiyopiya,+ munthu waulamuliro pansi pa Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Iye anali woyang’anira chuma chonse cha mfumukaziyo. Iyeyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu,+ 28 ndipo tsopano anali kubwerera kwawo. Ndunayi ili pa ulendo wobwerera kwawo itakhala m’galeta* lake, inali kuwerenga mokweza m’buku la mneneri Yesaya.+ 29 Ndiyeno mzimu unauza+ Filipo kuti: “Yandikira galeta lakelo uyende naye limodzi.” 30 Filipo anathamanga m’mbali mwa galetalo ndi kumumva akuwerenga mokweza m’buku la Yesaya mneneri. Ndipo Filipo anafunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” 31 Poyankha iye anati: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Pamenepo anachonderera Filipo kuti akwere ndi kukhala naye m’galetamo. 32 Ndime ya m’Malemba imene anali kuwerenga mokwezayo, mawu ake ndi awa: “Iye anamutengera kokamupha ngati nkhosa. Ngati mwana wa nkhosa wongokhala chete pamene akumumeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+ 33 Pamene anali kumuchitira zinthu zochititsa manyazi, anamuchotsera chiweruzo chomuyenera.+ Ndani angafotokoze tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo ake? Chifukwa moyo wake wachotsedwa padziko lapansi.”+
34 Poyankha nduna ija inauza Filipo kuti: “Ndiuzeni chonde, Kodi mneneriyu akunena za ndani? Za iye mwini kapena za munthu wina?” 35 Pamenepo Filipo, anayambira pa Lemba+ limeneli kumuuza uthenga wabwino wonena za Yesu.+ 36 Akuyenda choncho mumsewumo, anapeza madzi ambiri, ndipo nduna ija inati: “Taonani! Si awa madzi ambiri. Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?”+ 37* —— 38 Atatero analamula galetalo kuti liime. Ndipo onse awiri Filipo ndi nduna ija, anatsika ndi kulowa m’madzimo ndipo anaibatiza. 39 Atatuluka m’madzimo, mzimu wa Yehova unachotsa Filipo mwamsanga pamalopo,+ ndipo nduna ija sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala. 40 Koma Filipo anapezeka ali ku Asidodi, ndipo anayendayenda m’deralo ndi kulengeza+ uthenga wabwino m’mizinda yonse mpaka anafika ku Kaisareya.+
9 Koma Saulo anapitiriza kuopseza ophunzira+ a Ambuye komanso anali wofunitsitsa kuwapha.+ Choncho anapita kwa mkulu wa ansembe 2 kukamupempha zikalata za chilolezo zopita nazo kumasunagoge a ku Damasiko. Anapempha zikalatazo kuti akakapeza wina aliyense wotsatira Njirayo,*+ mwamuna kapena mkazi, akabwere naye ku Yerusalemu ali womangidwa.
3 Ali pa ulendo wakewo, anayandikira Damasiko. Mwadzidzidzi anangoona ngwee! kuwala kochokera kumwamba kutamuzungulira.+ 4 Pamenepo anagwa pansi ndipo anamva mawu akumuuza kuti: “Saulo, Saulo n’chifukwa chiyani ukundizunza?”+ 5 Iye anati: “Mbuyanga, ndinu ndani kodi?” Anamuyankha kuti: “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.+ 6 Komabe nyamuka,+ ulowe mumzindawo, ndipo ukauzidwa zoyenera kuchita.” 7 Amuna amene anali naye limodzi pa ulendowo,+ anangoima chilili kusowa chonena.+ Iwo anamva ndithu mawuwo,+ koma sanaone munthu aliyense. 8 Tsopano Saulo anaimirira, koma ngakhale anali atatsegula maso, sanali kuona chilichonse.+ Choncho anamugwira dzanja ndi kumulondolera njira ndipo analowa naye mu Damasiko. 9 Saulo anakhala masiku atatu osatha kuona,+ osadya kapena kumwa kanthu.
10 Mu Damasiko munali wophunzira wina dzina lake Hananiya.+ Ndiyeno Ambuye analankhula naye m’masomphenya kuti: “Hananiya!” Iye anayankha kuti: “Ine, Ambuye.” 11 Ambuyewo anamuuza kuti: “Nyamuka, upite kumsewu wotchedwa Msewu Wowongoka. Ukakafika panyumba ya Yudasi, ukafunse za munthu wa ku Tariso, dzina lake Saulo.+ Iyeyo akupemphera, 12 ndipo m’masomphenya waona munthu dzina lake Hananiya, amene anafika ndi kumuika manja kuti ayambenso kuona.”+ 13 Koma Hananiya anayankha kuti: “Ambuye, ndamva kwa anthu ambiri za munthu ameneyu. Ndamva zoipa zambiri zimene anachitira oyera anu ku Yerusalemu. 14 Ndipo panopo ansembe aakulu amupatsa mphamvu kuti amange onse oitana pa dzina lanu.”+ 15 Koma Ambuye anamuuza kuti: “Nyamuka uzipita, chifukwa munthu ameneyu ndi chiwiya changa chochita kusankhidwa+ chotengera dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina,+ komanso kwa mafumu+ ndi ana a Isiraeli. 16 Pakuti ndidzamuonetsa bwinobwino zopweteka zonse zimene ayenera kumva chifukwa cha dzina langa.”+
17 Choncho Hananiya anapita ndi kukalowa m’nyumbamo. Ndiyeno anamuika manja n’kunena kuti: “M’bale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene waonekera kwa iwe pamsewu umene wadzera, wandituma ine. Wandituma kwa iwe kuti uyambenso kuona ndi kutinso udzazidwe ndi mzimu woyera.”+ 18 Nthawi yomweyo m’maso mwa Saulo munagwa tinthu tooneka ngati mamba a nsomba, ndipo anayambanso kuona. Kenako anapita kukabatizidwa, 19 ndipo atadya chakudya anapezanso mphamvu.+
Kwa masiku angapo anakhala ndi ophunzira ku Damasiko.+ 20 Nthawi yomweyo anayamba kulalikira za Yesu m’masunagoge,+ kuti Ameneyu ndiye Mwana wa Mulungu. 21 Onse omumvetsera anadabwa kwambiri ndipo anali kunena kuti: “Kodi munthu uyu si uja anavutitsa koopsa+ oitana pa dzina limeneli a ku Yerusalemu? Kodi si chimenenso anabwerera kuno, kuti adzawagwire ndi kuwatengera kwa ansembe aakulu atawamanga?”+ 22 Koma Saulo anapitiriza kupeza mphamvu zambiri, ndipo anali kuthetsa nzeru Ayuda okhala mu Damasiko powafotokozera mfundo zomveka zotsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.+
23 Tsopano patapita masiku ambiri, Ayudawo anasonkhana pamodzi ndi kupangana zoti amuphe.+ 24 Koma chiwembu chawocho chinadziwika kwa Saulo. Komabe iwo anali kuyang’anira mosamala m’zipata zonse usana ndi usiku kuti amuphe.+ 25 Choncho usiku, ophunzira ake anamuika m’dengu ndi kumutulutsira pawindo la mpanda, n’kumutsitsira kunja.+
26 Atafika ku Yerusalemu+ anayesetsa kuti agwirizane ndi ophunzira kumeneko. Koma onse ankamuopa, chifukwa sanakhulupirire kuti anali wophunzira. 27 Choncho Baranaba anamuthandiza+ mwa kupita naye kwa atumwi. Kumeneko iye anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Saulo anaonera Ambuye+ amene analankhula naye pamsewu.+ Anawafotokozeranso mmene Saulo analankhulira molimba mtima ku Damasiko+ m’dzina la Yesu. 28 Pamenepo anapitiriza kukhala nawo, n’kumayenda momasuka mu Yerusalemu, ndiponso anali kulankhula molimba mtima m’dzina la Ambuye.+ 29 Ndipo anali kulankhulana ndi kutsutsana ndi Ayuda olankhula Chigiriki. Koma iwo anayesa kupeza njira yoti amuphere.+ 30 Abale atazindikira zimenezi, anam’tengera ku Kaisareya ndi kumutumiza ku Tariso.+
31 Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira.
32 Tsopano pamene Petulo anali kuyendayenda m’madera onse, anafikanso kwa oyera amene anali kukhala ku Luda.+ 33 Kumeneko anapeza munthu wina dzina lake Eneya. Popeza kuti anali wakufa ziwalo, anakhala ali chigonere pabedi lake kwa zaka 8. 34 Ndiyeno Petulo anamuuza kuti:+ “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa.+ Dzuka ndi kuyala bwino bedi lakoli.” Nthawi yomweyo anadzuka. 35 Onse okhala mu Luda ndi m’chigwa cha Sharoni+ anamuona, ndipo anatembenukira kwa Ambuye.+
36 Koma ku Yopa+ kunali wophunzira wina dzina lake Tabita, dzina limene polimasulira limatanthauza Dorika.* Tabita anali kuchita ntchito zabwino zambiri,+ ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka. 37 Ndipo m’masiku amenewo iye anadwala n’kumwalira. Choncho anamusambitsa ndi kumugoneka m’chipinda cham’mwamba. 38 Popeza kuti Luda anali pafupi ndi Yopa,+ ophunzirawo atamva kuti Petulo ali mumzinda umenewu, anatumiza amuna awiri kukamudandaulira kuti: “Chonde mufike kwathuku msanga.” 39 Pamenepo Petulo ananyamuka n’kupita nawo limodzi. Atafika kumeneko, iwo anamutengera m’chipinda cham’mwamba chija. Ndipo akazi onse amasiye anabwera kwa iye akulira ndi kumuonetsa malaya ambiri akunja ndi amkati+ amene Dorika anali kusoka pamene anali nawo.+ 40 Koma Petulo anatulutsa anthu onse,+ ndiyeno anagwada pansi ndi kupemphera. Kenako anatembenukira mtembowo ndi kunena kuti: “Tabita, dzuka!” Pamenepo mayiyo anatsegula maso ake, ndipo mmene anaona Petulo, anadzuka n’kukhala tsonga.+ 41 Tsopano Petulo anamupatsa dzanja lake ndi kumuimiritsa.+ Atatero anaitana oyerawo ndi akazi amasiye aja, ndipo anamupereka kwa iwo ali wamoyo.+ 42 Izi zinadziwika mu Yopa monse, ndipo ambiri anakhala okhulupirira mwa Ambuye.+ 43 Kwa masiku angapo Petulo anakhalabe mu Yopa+ kwa munthu wina wofufuta zikopa, dzina lake Simoni.+
10 Tsopano ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Koneliyo, kapitawo wa gulu la asilikali+ lotchedwa Ataliyana.+ 2 Iyeyu anali wopembedza+ ndi woopa+ Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse. Anali kupatsa anthu mphatso zambiri zachifundo+ ndipo anali kupemphera kwa Mulungu nthawi zonse.+ 3 Tsiku lina cha m’ma 3 koloko masana,*+ anaona mngelo+ wa Mulungu m’masomphenya.+ Mngeloyo anabwera kwa iye n’kunena kuti: “Koneliyo!” 4 Pamenepo Koneliyo anayang’anitsitsa mngelo uja, ndipo mantha atamugwira anati: “N’chiyani Mbuyanga?” Mngeloyo anamuuza kuti: “Mapemphero ako+ ndi mphatso zako zachifundo zakwera kwa Mulungu monga chikumbutso.+ 5 Chotero tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina dzina lake Simoni, wotchedwanso Petulo. 6 Munthu ameneyu ndi mlendo kunyumba kwa Simoni wina wofufuta zikopa, amene nyumba yakeyo ili m’mbali mwa nyanja.”+ 7 Mngelo amene anali kulankhula nayeyo atangochoka, iye anaitana antchito ake a panyumbapo awiri ndi msilikali. Msilikaliyo anali wopembedza, ndipo anali mmodzi wa amene anali kumutumikira nthawi zonse.+ 8 Koneliyo anawafotokozera zonse ndi kuwatuma ku Yopa.+
9 Tsiku lotsatira, ulendo wawo uli mkati komanso akuyandikira mzindawo, Petulo anakwera padenga*+ kukapemphera cha m’ma 12 koloko masana.*+ 10 Koma anamva njala kwambiri ndipo anafuna kudya. Pamene chakudya chinali kukonzedwa, anayamba kuona masomphenya.+ 11 M’masomphenyawo anaona kumwamba kutatseguka,+ ndipo chinthu china chake chinali kutsika. Chinthucho chinali chooneka ngati chinsalu chachikulu chimene achigwira m’makona onse anayi n’kumachitsitsira padziko lapansi. 12 Pachinthu chimenecho panali mitundu yonse ya nyama za miyendo inayi, ndi zokwawa zapadziko lapansi, ndiponso mbalame zam’mlengalenga.+ 13 Pamenepo mawu anamveka kwa iye kuti: “Nyamuka Petulo, ipha udye!”+ 14 Koma Petulo anati: “Iyayi Ambuye, sindinadyepo choipitsidwa ndi chonyansa chilichonse chikhalire.”+ 15 Ndipo mawu aja anamvekanso kwa iye kachiwiri kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.”+ 16 Mawu amenewo anamvekanso kachitatu, ndipo nthawi yomweyo chinthu chooneka ngati chinsalu chija chinatengedwa kupita kumwamba.+
17 Petulo atathedwa nzeru chifukwa chosamvetsa tanthauzo la masomphenya amene anaonawo, amuna otumidwa ndi Koneliyo aja anali atafunsira kuti nyumba ya Simoni ili kuti ndipo anali ataima pachipata.+ 18 Iwo analankhula mofuula ndi kufunsa ngati kumeneko anali ndi mlendo dzina lake Simoni wotchedwanso Petulo. 19 Petulo ali mkati moganizira za masomphenyawo, mzimu+ unati: “Tamvera! Pali amuna atatu amene akukufuna. 20 Chotero nyamuka, tsika upite nawo limodzi, usakayikire ayi, chifukwa ndawatuma ndine.”+ 21 Choncho Petulo anatsika kukakumana ndi anthuwo ndipo anati: “Amene mukumufunayo ndine. Mukufuna chiyani kuno?” 22 Iwo anati: “Tachokera kwa Koneliyo, kapitawo wa asilikali. Iye ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu,+ amene mtundu wonse wa Ayuda umamuyamikira.+ Mngelo woyera anamupatsa malangizo a Mulungu kuti atume anthu kudzakutengani kuti mupite kunyumba kwake, akamve zimene inu mukanene.” 23 Ndiyeno anawalowetsa m’nyumba ndi kuwachereza.
M’mawa mwake ananyamuka ndi kupita nawo, ndipo abale ena a mu Yopa anatsagana naye. 24 Tsiku linalo anafika ku Kaisareya. Kumeneko Koneliyo anali kuwayembekezera, ndipo anasonkhanitsa achibale ndi mabwenzi ake apamtima. 25 Pamene Petulo anali kulowa, Koneliyo anakumana naye ndipo anagwada pamaso pake n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. 26 Koma Petulo anamuimiritsa, ndi kunena kuti: “Imirira, inenso ndine munthu chabe.”+ 27 Pamene anali kukambirana naye, analowa mkati ndipo anapeza anthu ambiri atasonkhana mmenemo. 28 Ndiyeno Petulo anawauza kuti: “Inunso mukudziwa bwino kuti n’kosaloleka kuti Myuda azicheza ndi munthu wa fuko lina kapena kumuyandikira.+ Koma tsopano Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti woipitsidwa kapena wonyansa.+ 29 N’chifukwa chake ndabwera mosanyinyirika mutanditumizira anthu aja. Choncho ndikufuna ndidziwe chimene mwandiitanira.”
30 Pamenepo Koneliyo anati: “Masiku anayi apitawo kuchokera pa ola lino, ndinali kupemphera m’nyumba mwanga cha m’ma 3 koloko masana.+ Mwadzidzidzi munthu wovala zowala+ anaimirira pamaso panga. 31 Munthuyo anandiuza kuti, ‘Koneliyo, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira mphatso zako zachifundo.+ 32 Chotero tumiza anthu ku Yopa, kuti akaitane Simoni wotchedwanso Petulo.+ Munthu ameneyo ndi mlendo m’nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, amene amakhala m’mbali mwa nyanja.’+ 33 Chotero ndinawatumiza mwamsanga kwa inu, ndipo mwachita bwino kubwera kuno. N’chifukwa chake pa nthawi ino tonse tili pano pamaso pa Mulungu, kuti timve zonse zimene Yehova wakulamulani kuti mutiuze.”+
34 Pamenepo Petulo anayamba kulankhula kuti: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho.+ 35 Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.+ 36 Mulungu anatumiza mawu+ kwa ana a Isiraeli ndi kulengeza kwa iwo uthenga wabwino wa mtendere+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ameneyu ndiye Ambuye wa ena onse.+ 37 Inu mukudziwa nkhani imene inali m’kamwam’kamwa mu Yudeya monse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane anali kulalikira.+ 38 Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, kuti Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye,+ anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.+ 39 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zonse zimene anachita m’dziko la Ayuda ndi mu Yerusalemu momwe. Koma iwo anamupha mwa kumupachika pamtengo.+ 40 Ameneyu Mulungu anamuukitsa tsiku lachitatu ndi kumulola kuonekera,+ 41 osati kwa anthu onse, koma kwa mboni zoikidwiratu ndi Mulungu,+ zomwe ndi ife amene tinadya ndi kumwa naye limodzi+ atauka kwa akufa. 42 Ndiponso, anatilamula kuti tilalikire+ kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira wakuti iyeyu ndi Amene Mulungu anamuika kukhala woweruza anthu amoyo ndi akufa.+ 43 Aneneri onse amachitira umboni za iyeyu,+ kuti aliyense womukhulupirira, machimo ake amakhululukidwa m’dzina lake.”+
44 Pamene Petulo anali kulankhula zinthu izi, mzimu woyera unagwa pa onse amene anali kumvera mawu amenewo.+ 45 Ndipo okhulupirika amene anabwera ndi Petulo, amene anali odulidwa anadabwa, chifukwa mphatso yaulere ya mzimu woyera inalinso kuthiridwa pa anthu a mitundu ina.+ 46 Pakuti anawamva akulankhula m’malilime ndi kulemekeza Mulungu.+ Ndiyeno Petulo anati: 47 “Anthu awa alandira mzimu woyera monga mmenenso ife tinalandirira. Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe ndi madzi?”+ 48 Atatero anawalamula kuti abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu.+ Pamenepo iwo anamupempha kuti akhalebe nawo masiku angapo.
11 Tsopano atumwi ndi abale amene anali mu Yudeya anamva kuti anthu a mitundu ina+ nawonso alandira mawu a Mulungu. 2 Choncho Petulo atapita ku Yerusalemu, olimbikitsa mdulidwe+ anayamba kutsutsana naye. 3 Iwo anali kumunena kuti anakalowa m’nyumba ya anthu osadulidwa ndi kudya nawo. 4 Pamenepo Petulo anayamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene zinachitika, kuti:
5 “Ndinali kupemphera mumzinda wa Yopa. Ndipo ndinayamba kuona masomphenya. M’masomphenyawo ndinaona chinthu chikutsika. Chinthucho chinali chooneka ngati chinsalu chachikulu chimene achigwira m’makona onse anayi, ndipo anali kuchitsitsa kuchokera kumwamba moti chinafika kwa ine. 6 Nditayang’anitsitsa m’chinthucho, ndinaonamo nyama za miyendo inayi zapadziko lapansi, zilombo zakutchire, zokwawa komanso mbalame zam’mlengalenga.+ 7 Ndinamvanso mawu akundiuza kuti, ‘Nyamuka Petulo, ipha udye!’+ 8 Koma ine ndinati, ‘Iyayi Ambuye, m’kamwa mwangamu simunalowepo choipitsidwa ndi chonyansa chilichonse chiyambire.’+ 9 Poyankha, mawu ochokera kumwambawo anamveka kachiwiri kuti, ‘Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.’+ 10 Mawu amenewo anamvekanso kachitatu, ndipo zonse zinakwezedwanso kumwamba.+ 11 Nthawi yomweyo, amuna atatu amene anatumidwa kwa ine kuchokera ku Kaisareya anaima panyumba imene tinali kukhala.+ 12 Chotero mzimu+ unandiuza kuti ndipite nawo, ndisakayikire ngakhale pang’ono. Pamenepo abale 6 awa anatsagana nane, ndipo tinakalowa m’nyumba ya munthuyo.+
13 “Iye anatiuza mmene anaonera mngelo ataimirira m’nyumba yake ndi kunena kuti, ‘Tuma anthu kuti apite ku Yopa akaitane Simoni wotchedwanso Petulo.+ 14 Iye adzalankhula nawe zinthu zimene zidzathandize iwe ndi banja lako lonse kupulumuka.’+ 15 Koma nditangoyamba kulankhula, mzimu woyera unawagwera monga mmene unachitiranso pa ife poyamba paja.+ 16 Zitatero ndinakumbukira mawu a Ambuye aja akuti, ‘Yohane anabatiza ndi madzi,+ koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.’+ 17 Chotero ngati Mulungu anapereka mphatso yaulere imodzimodziyo kwa iwo, monga mmenenso anachitira kwa ife amene tinakhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu,+ ine ndine ndani kuti ndiletse Mulungu?”+
18 Tsopano pamene iwo anamva zimenezi, anangovomereza,+ ndipo anatamanda Mulungu+ kuti: “Chabwino, pamenepa ndiye kuti Mulungu wapereka mwayi kwa anthu a mitundu ina kuti iwonso alape ndi kudzapeza moyo.”+
19 Ndiyeno anthu amene anabalalika+ chifukwa cha chisautso chimene chinagwera Sitefano anayenda mpaka ku Foinike,+ ku Kupuro+ ndi ku Antiokeya. Ndipo sanali kulalikira mawu kwa wina aliyense koma kwa Ayuda okha.+ 20 Koma pakati pawo panali amuna ena a ku Kupuro ndi ku Kurene. Amenewa atafika ku Antiokeya anayamba kulankhula ndi anthu olankhula Chigiriki,+ ndipo anali kulengeza kwa iwo uthenga wabwino wa Ambuye Yesu.+ 21 Apanso, dzanja la Yehova+ linali nawo, ndipo ambiri amene anakhulupirira anatembenukira kwa Ambuye.+
22 Mpingo wa ku Yerusalemu unamva za iwo, ndipo unatumiza Baranaba+ kuti apite ku Antiokeya. 23 Atafika kumeneko ndi kuona kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu, anakondwera+ ndipo anayamba kulimbikitsa onse kuti apitirize kukhala okhulupirika kwa Ambuye motsimikiza mtima.+ 24 Baranaba anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi mzimu woyera komanso wachikhulupiriro. Ndipo khamu lalikulu ndithu linakhulupirira Ambuye.+ 25 Kenako Baranaba anapita ku Tariso+ kukafufuza Saulo+ 26 ndipo atamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Choncho iwo anasonkhana ndi mpingo kumeneko chaka chonse, ndipo anaphunzitsa anthu ambirimbiri. Ku Antiokeya, n’kumene ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.+
27 M’masiku amenewa aneneri+ anapita ku Antiokeya kuchokera ku Yerusalemu. 28 Mmodzi wa iwo dzina lake Agabo,+ analosera mwa mzimu kuti padziko lonse lapansi kumene kuli anthu,+ padzagwa njala yaikulu. Izi zinachitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo. 29 Chotero aliyense wa ophunzirawo, anatsimikiza mtima kutumiza thandizo+ lililonse limene akanatha+ kwa abale okhala ku Yudeya. 30 Ndipo anachitadi zimenezo mwa kutumiza thandizolo kwa akulu, kudzera mwa Baranaba ndi Saulo.+
12 Nthawi imeneyo m’pamene Mfumu Herode* anayamba kuzunza+ ena a mumpingo. 2 Yakobo m’bale wake wa Yohane+ anamupha ndi lupanga.+ 3 Ataona kuti zimenezi zasangalatsa Ayuda,+ anamanganso Petulo. (Amenewa anali masiku a mikate yopanda chofufumitsa.)+ 4 Atamugwira, anamutsekera m’ndende+ ndipo anamupereka m’manja mwa magulu anayi a asilikali, kuti azisinthana pomulondera. Gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Cholinga cha Herode chinali chakuti adzamuonetse kwa anthu pambuyo pa pasika.+ 5 Chotero Petulo anakhala akusungidwa m’ndendemo, koma mpingo unali kumupempherera+ mosalekeza kwa Mulungu ndi mtima wonse.
6 Tsopano Herode atakonzeka kuti abweretse Petulo kwa anthu, usiku umenewo Petuloyo anali chigonere ali womangidwa ndi maunyolo awiri pakati pa asilikali awiri. Pakhomo panalinso alonda olondera ndende. 7 Mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova anaimirira+ chapafupi, ndipo kuwala kunaunika m’chipinda cha ndendecho. Kenako mngeloyo anadzutsa Petulo mwa kumugunda m’nthiti,+ n’kunena kuti: “Dzuka msanga!” Pamenepo maunyolo amene anamumanga nawo manjawo anagwa pansi.+ 8 Ndiyeno mngeloyo+ anamuuza kuti: “Konzeka ndipo uvale nsapato zako.” Iye anachita zimenezo. Kenako anamuuza kuti: “Vala malaya ako akunja+ ndipo uzinditsatira.” 9 Pamenepo anatuluka ndi kumamutsatira, koma iye sanadziwe kuti zimene zinali kuchitika ndi mngelozo zinali zenizeni. Ankangoganiza kuti akuona masomphenya.+ 10 Atapitirira gulu loyamba la asilikali a pachipata ndi lachiwiri, anafika pachipata chachitsulo cholowera mumzinda, ndipo chinawatsegukira chokha.+ Pamene anatuluka anayendera limodzi msewu umodzi wokha, ndipo nthawi yomweyo mngelo uja anamuchokera. 11 Koma Petulo nzeru zitamubwerera, anati: “Ndadziwa tsopano kuti Yehova ndiye watumiza mngelo wake+ kudzandilanditsa+ m’manja mwa Herode, komanso kudzandilanditsa ku zonse zimene anthu achiyuda anali kuyembekezera.”
12 Ataganizira zimene zinachitikazo, iye anapita kunyumba ya Mariya, mayi wake wa Yohane wotchedwanso Maliko.+ Kumeneko anthu ambiri anali atasonkhana pamodzi ndipo anali kupemphera. 13 Pamene anagogoda pachitseko cha pachipata, mtsikana wantchito dzina lake Roda anapita kuti akaone amene akugogoda. 14 Koma atazindikira mawu a Petulo, sanatsegule chipatacho chifukwa cha chimwemwe. M’malomwake, anathamangira mkati ndi kukanena kuti Petulo waima pachipata. 15 Iwo anamunena kuti: “Wachita misala eti!” Koma iye analimbikira kunena motsimikiza kuti akunena zoona. Iwo tsopano anayamba kunena kuti: “Ndi mngelo wake ameneyo.”+ 16 Koma Petulo anapitiriza kugogoda. Iwo atatsegula, anamuona ndipo anadabwa kwambiri. 17 Koma iye anawakwezera dzanja+ kuti akhale chete, ndipo anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Yehova anamutulutsira m’ndende. Kenako iye anati: “Zinthu zimenezi mukazifotokoze kwa Yakobo+ ndi kwa abale.” Atatero anatuluka n’kupita kumalo ena.
18 Tsopano kutacha,+ panali chipwirikiti pakati pa asilikali aja posadziwa chimene chachitikira Petulo. 19 Herode+ anafunafuna Petulo pena paliponse, ndipo atalephera kumupeza, anapanikiza alondawo ndi mafunso ndi kulamula kuti awatenge, akawapatse chilango.+ Pamenepo Herode anachoka ku Yudeya ndi kupita ku Kaisareya, kumene anakhalako kanthawi ndithu.
20 Tsopano Herode anali wokwiya ndi anthu a ku Turo ndi ku Sidoni, ndipo anafuna kuwathira nkhondo. Choncho onse anabwera kwa iye mogwirizana. Ndipo iwo atanyengerera Balasito, amene anali woyang’anira chipinda chogona cha mfumu, anayamba kupempha mtendere. Iwo anachita zimenezi chifukwa dziko lawo linali kudalira chakudya+ chochokera m’dziko la mfumuyo. 21 Koma pa tsiku loikidwiratu, Herode anavala zovala zake zachifumu ndi kukhala pampando wake woweruzira milandu, ndi kuyamba kulankhula nawo. 22 Anthu osonkhanawo atamva mawu ake anayamba kufuula kuti: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu ayi!”+ 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha,+ chifukwa sanapereke ulemerero kwa Mulungu.+ Ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalira.
24 Koma mawu+ a Yehova anapitiriza kukula ndi kufalikira.+
25 Tsopano Baranaba+ ndi Saulo atamaliza utumiki wopereka thandizo+ ku Yerusalemu, anabwerera ndi kutenga Yohane,+ wotchedwanso Maliko.
13 Tsopano mumpingo wa ku Antiokeya munali aneneri+ ndi aphunzitsi. Iwo anali Baranaba, Sumeoni wotchedwa Nigeri, Lukiyo+ wa ku Kurene, Manayeni amene anaphunzira pamodzi ndi Herode wolamulira chigawo, ndi Saulo. 2 Pamene anali kutumikira+ Yehova ndi kusala kudya, mzimu woyera unati: “Mwa anthu onse, mundipatulire Baranaba ndi Saulo+ kuti agwire ntchito imene ndinawaitanira.” 3 Pamenepo anasala kudya ndipo anapemphera, kenako anawaika manja+ ndi kuwalola kuti apite.
4 Chotero amuna awa, amene mzimu woyera unawatumiza, anapita ku Selukeya, ndipo kuchokera kumeneko ananyamuka ulendo wa pamadzi wopita ku Kupuro. 5 Atafika kumeneko, mumzinda wa Salami anayamba kufalitsa mawu a Mulungu m’masunagoge a Ayuda. Iwo analinso ndi Yohane+ monga wowatumikira.
6 Iwo anayenda pachilumba chonsecho mpaka kukafika ku Pafo. Kumeneko anakumana ndi munthu wina wamatsenga. Munthu ameneyu anali Myuda dzina lake Bara-Yesu, ndipo analinso mneneri wonyenga.+ 7 Iyeyu anali limodzi ndi bwanamkubwa Serigio Paulo, munthu wanzeru. Bwanamkubwayu anaitana Baranaba ndi Saulo, chifukwa anali kufunitsitsa kumva mawu a Mulungu. 8 Koma Elima, wamatsenga, (uku ndiye kumasulira kwa dzina lakeli) anayamba kutsutsana nawo.+ Iye anali kuyesetsa kuti bwanamkubwayo asakhulupirire Ambuye. 9 Saulo, wotchedwanso Paulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera, anamuyang’anitsitsa 10 n’kunena kuti: “Iwe munthu wodzazidwa ndi mtundu uliwonse wa chinyengo ndi zoipa, mwana wa Mdyerekezi,+ mdani wa chilichonse cholungama, kodi sudzaleka kupotoza njira zowongoka za Yehova? 11 Tsopano tamvera! Dzanja la Yehova lili pa iwe, ndipo ukhala wakhungu. Kwa kanthawi, suthanso kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo nkhungu yamphamvu ndi mdima wandiweyani zinamugwera, ndipo anafufuza uku ndi uku kufuna anthu oti amugwire dzanja ndi kumutsogolera.+ 12 Bwanamkubwa+ uja ataona zimenezo, anakhala wokhulupirira, pakuti anadabwa kwambiri ndi zimene anaphunzira zokhudza Yehova.
13 Tsopano amunawo, pamodzi ndi Paulo, anayamba ulendo wa panyanja kuchoka ku Pafo, ndipo anafika ku Pega, ku Pamfuliya.+ Koma Yohane+ anawasiya ndi kubwerera+ ku Yerusalemu. 14 Iwo anapitiriza ulendo wawo kuchokera ku Pega ndi kukafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa m’sunagoge+ tsiku la sabata ndi kukhala pansi. 15 Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zitawerengedwa pamaso pa anthu,+ atsogoleri+ a sunagoge anawatumizira mawu akuti: “Amuna inu, abale athu, ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.” 16 Choncho Paulo anaimirira, ndipo anakweza dzanja+ lake ndi kunena kuti:
“Anthu inu, Aisiraeli, ndi ena nonse oopa Mulungu, tamverani.+ 17 Mulungu wa anthu awa Aisiraeli, anasankha makolo athu akale. Anakweza anthu amenewa pamene anali kukhala m’dziko lachilendo la Iguputo, ndipo anawatulutsa mmenemo ndi dzanja lokwezeka.+ 18 Kwa nthawi ya zaka pafupifupi 40,+ anapirira khalidwe lawo m’chipululu. 19 Ndipo atawononga mitundu 7 m’dziko la Kanani, anagawa dzikolo kwa Aisiraeli mwa kuchita maere.+ 20 Zonsezi zinachitika m’zaka pafupifupi 450.
“Zimenezi zitatha anawapatsa oweruza mpaka kudzafika pa mneneri Samueli.+ 21 Koma kuchokera pamenepo anthuwo ananena kuti akufuna mfumu.+ Chotero Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini,+ ndipo anakhala mfumu yawo kwa zaka 40. 22 Atamuchotsa ameneyu,+ anawapatsa Davide monga mfumu yawo.+ Iyeyu Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Jese,+ munthu wapamtima panga.+ Ameneyu adzachita zonse zimene ine ndikufuna.’+ 23 Kuchokera mwa ana+ a munthu ameneyu, malinga ndi lonjezo lake, Mulungu wabweretsa mpulumutsi mu Isiraeli,+ amene ndi Yesu. 24 Mpulumutsi+ ameneyu asanafike, Yohane+ anali atalalikiriratu poyera kwa anthu onse mu Isiraeli za ubatizo, monga chizindikiro cha kulapa. 25 Koma pamene Yohane anali kukwaniritsa utumiki wake, anali kunena kuti, ‘Kodi mukuganiza kuti ine ndine ndani? Amene inu mukumuganizira si ine ayi. Koma wina akubwera pambuyo panga, amene ine sindili woyenera kumumasula nsapato kumapazi kwake.’+
26 “Amuna inu, abale anga, inu ana a mbadwa za Abulahamu, ndi ena onse oopa Mulungu amene ali pakati panu, mawu a chipulumutso chimenechi atumizidwa kwa ife.+ 27 Pakuti okhala mu Yerusalemu ndi olamulira awo sanamudziwe Iyeyu.+ Koma pochita ngati oweruza, anakwaniritsa zinthu zonenedwa ndi Aneneri,+ zimene zimawerengedwa mokweza Sabata lililonse. 28 Ngakhale kuti sanapeze chifukwa chomuphera,+ anaumiriza Pilato kuti ameneyu anyongedwe basi.+ 29 Ndiyeno iwo atakwaniritsa zinthu zonse zolembedwa zonena za iye,+ anamutsitsa pamtengo+ ndi kumuika m’manda achikumbutso.+ 30 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa.+ 31 Ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anatsagana naye popita ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amene tsopano ndiwo mboni zake kwa anthu.+
32 “Chotero ife tikulengeza kwa inu uthenga wabwino wa lonjezo limene linaperekedwa kwa makolo athu.+ 33 Uthengawo ndi wakuti Mulungu wakwaniritsa lonjezo lonselo kwa ife ana awo mwa kuukitsa Yesu.+ Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene zinalembedwa mu salimo lachiwiri kuti, ‘Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala Atate wako.’+ 34 Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa kwa akufa, osayembekezera kubwereranso kuthupi limene lingathe kuvunda, anaitchula motere, ‘Ine ndidzakusonyezani anthu inu kukoma mtima kwanga kosatha ndi kokhulupirika, kumene ndinasonyeza Davide.’+ 35 Ndipo mu salimo lina akunenanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.’+ 36 Koma Davide+ anakwaniritsa chifuniro cha Mulungu mu nthawi ya m’badwo wake, ndipo anagona mu imfa ndi kuikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake, moti thupi lake linavunda.+ 37 Komatu amene Mulungu anamuukitsa uja thupi lake silinavunde.+
38 “Chotero dziwani abale anga kuti, ife tikulalikira kwa inu za kukhululukidwa kwa machimo kudzera mwa Iyeyu.+ 39 Dziwaninso kuti pa zinthu zonse zimene kunali kosatheka kuti muyesedwe opanda mlandu kudzera m’chilamulo cha Mose,+ aliyense wokhulupirira akuyesedwa wopanda mlandu kudzera mwa Iyeyu.+ 40 Chotero samalani kuti zimene Zolemba za aneneri zikunena zisakugwereni. Zolemba za anenerizo zikuti, 41 ‘Inu onyoza zimene ine ndikuchita, mudzaona zimene ndikuchitazo ndi kudabwa nazo. Kenako mudzazimiririka, chifukwa simudzakhulupirira ngakhale pang’ono zimene ndidzachite m’masiku anu, ngakhale wina atakufotokozerani mwatsatanetsatane.’”+
42 Tsopano pamene anali kutuluka, anthu anayamba kuwachonderera kuti adzawauzenso nkhani zimenezi sabata lotsatira.+ 43 Choncho msonkhano wa m’sunagoge utatha, Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda ambiri amene anali kupembedza Mulungu anatsatira Paulo ndi Baranaba.+ Ndipo iwo polankhula ndi anthuwo anawalimbikitsa+ kuti apitirize kuyenda m’kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+
44 Sabata lotsatira, pafupifupi mzinda wonse unasonkhana pamodzi kudzamvera mawu a Yehova.+ 45 Ayuda ataona khamu la anthulo, anachita nsanje+ ndipo anayamba kutsutsa mwamwano zimene Paulo anali kulankhula.+ 46 Chotero Paulo ndi Baranaba analankhula molimba mtima kuti: “Kunali koyenera kuti inu mukhale oyamba kuuzidwa mawu a Mulungu.+ Koma popeza kuti mukuwatayira kumbali+ ndipo mukudziweruza nokha kukhala osayenera moyo wosatha, ifeyo tikutembenukira kwa anthu a mitundu ina.+ 47 Ndipotu Yehova anatiikira lamulo lakuti, ‘Ndakuikani monga kuwala kwa anthu a mitundu ina,+ kuti mukhale chipulumutso mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’”+
48 Pamene anthu a mitundu inawo anamva zimenezi, anakondwera ndi kutamanda mawu a Yehova.+ Ndipo onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.+ 49 Komanso, mawu a Yehova anapitirira kufalitsidwa m’dziko lonselo.+ 50 Koma Ayuda+ anauza zoipa amayi otchuka amene anali opembedza Mulungu, komanso amuna olemekezeka a mumzindawo. Chotero iwowa anachititsa kuti Paulo ndi Baranaba ayambe kuzunzidwa,+ ndipo anawaponya kunja kwa mzinda wawo. 51 Koma Paulo ndi Baranaba anasansira anthuwo fumbi kumapazi awo+ n’kupita ku Ikoniyo. 52 Ndipo ophunzirawo anapitiriza kudzazidwa ndi chimwemwe+ ndi mzimu woyera.
14 Tsopano Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo,+ analowa m’sunagoge+ wa Ayuda. Mmenemo analankhula bwino kwambiri moti khamu lalikulu la Ayuda limodzi ndi Agiriki+ anakhala okhulupirira. 2 Koma Ayuda amene sanakhulupirire, anauza zoipa+ anthu a mitundu ina ndi kupotoza maganizo awo kuti atsutsane ndi abalewo.+ 3 Chotero kwa nthawi yaitali, anakhala akulankhula molimba mtima chifukwa cha mphamvu ya Yehova. Iye anatsimikizira mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu, mwa kulola kuti zizindikiro ndi zodabwitsa zichitike kudzera mwa ophunzirawo.+ 4 Koma khamu la mumzindawo linagawanika. Ena anakhala kumbali ya Ayuda, ena kumbali ya atumwi. 5 Ndiyeno anthu a mitundu ina komanso Ayuda pamodzi ndi olamulira awo, anakonza chiwembu kuti achitire chipongwe atumwiwo ndi kuwaponya miyala.+ 6 Koma iwo atadziwitsidwa zimenezi, anathawira+ m’mizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi m’madera ozungulira. 7 Kumeneko anapitiriza kulengeza uthenga wabwino.+
8 Tsopano ku Lusitara, mwamuna wina wolumala miyendo anali atakhala pansi. Iyeyu anabadwa wolumala ndipo anali asanayendepo chibadwire.+ 9 Mwamuna ameneyu anali kumvetsera pamene Paulo anali kulankhula. Ndiyeno Paulo atamuyang’anitsitsa anaona kuti ali ndi chikhulupiriro+ ndipo angathe kuchiritsidwa. 10 Choncho Paulo analankhula mokweza mawu kuti: “Imirira ndi miyendo yako!” Pamenepo iye anadumpha n’kuyamba kuyenda.+ 11 Pamene khamu la anthu linaona zimene Paulo anachitazo, linafuula ndi kunena m’chinenero cha Chilukaoniya kuti: “Milungu+ yakhala ngati anthu, ndipo yatsikira kwa ife!” 12 Chotero Baranaba anayamba kumutchula kuti Zeu, koma Paulo anamutchula kuti Heme, chifukwa ndi amene anali kutsogolera polankhula. 13 Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kachisi wake anali pafupi kunja kwa mzindawo, anabweretsa ng’ombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa kuzipata. Iye pamodzi ndi khamu la anthulo anali kufuna kupereka nsembe.+
14 Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anang’amba malaya awo akunja ndi kuthamanga kukalowa m’khamu la anthu lija akufuula 15 kuti: “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu+ okhala ndi zofooka+ ngati inu nomwe, ndipo tikulengeza uthenga wabwino kwa inu. Tikuchita izi kuti musiye zachabechabe zimenezi+ ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo,+ amene anapanga kumwamba,+ dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo. 16 M’mibadwo ya m’mbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuyenda m’njira zawo.+ 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino.+ Anakupatsani mvula+ kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”+ 18 Ngakhale kuti atumwiwo ananena mawu amenewa, anavutikabe kuti aletse khamu la anthulo kupereka nsembe kwa iwo.
19 Ndiyeno Ayuda anafika kuchokera ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo ndipo anakopa anthuwo.+ Choncho anaponya Paulo miyala ndi kumukokera kunja kwa mzindawo, poganiza kuti wafa.+ 20 Koma pamene ophunzira anamuzungulira, anadzuka ndi kukalowa mumzinda. Tsiku lotsatira iye pamodzi ndi Baranaba anachoka ndi kupita ku Debe.+ 21 Atalengeza uthenga wabwino mumzinda umenewo ndi kuphunzitsa anthu angapo kuti akhale ophunzira,+ anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya. 22 M’malo onsewa anali kulimbitsa mitima ya ophunzira+ ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’chikhulupiriro. Anali kuwauza kuti: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”+ 23 Komanso, anawaikira akulu+ mumpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya,+ anawapereka kwa Yehova+ yemwe anamukhulupirira.
24 Kenako anadutsa ku Pisidiya ndi kukalowa ku Pamfuliya.+ 25 Atalengeza mawu opatulika ku Pega, anapita ku Ataliya. 26 Pochoka kumeneko anayenda ulendo wa pamadzi wobwerera ku Antiokeya.+ Kumeneku n’kumene m’mbuyomo abale anawaika m’manja mwa Mulungu kuti awasonyeze kukoma mtima kwakukulu n’cholinga choti agwire ntchito imene tsopano anali ataikwaniritsa.+
27 Atafika kumeneko ndi kusonkhanitsa pamodzi mpingo, anafotokoza+ zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo. Anafotokozanso kuti Mulungu anatsegulira anthu a mitundu ina khomo lolowera m’chikhulupiriro chimenechi.+ 28 Choncho anakhala ndi ophunzirawo kwa kanthawi ndithu.
15 Ndiyeno amuna ena ochokera ku Yudeya+ anapita kumeneko ndi kuyamba kuphunzitsa abale kuti: “Mukapanda kudulidwa+ malinga ndi mwambo wa Mose,+ simungapulumuke.” 2 Koma Paulo ndi Baranaba sanamvane nawo ndipo anatsutsana nawo kwambiri. Choncho iwo anasankha Paulo ndi Baranaba, pamodzi ndi ena mwa iwo, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,+ kuti akawauze za kutsutsanako.
3 Tsopano mpingo utawaperekeza,+ amuna amenewa anapitiriza ulendo wawo kudzera ku Foinike ndi ku Samariya. Kumeneko anali kufotokoza mwatsatanetsatane za kutembenuka kwa anthu a mitundu ina,+ ndipo iwo anasangalatsa kwambiri abale onse.+ 4 Atafika ku Yerusalemu analandiridwa ndi manja awiri+ ndi mpingo, atumwi, komanso akulu. Kumeneko anafotokoza zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.+ 5 Koma okhulupirira ena, amene kale anali m’gulu lampatuko la Afarisi anaimirira m’mipando yawo n’kunena kuti: “M’pofunika kuwadula+ ndi kuwalamula kuti azisunga chilamulo cha Mose.”+
6 Ndiyeno atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti akambirane nkhani imeneyi.+ 7 Tsopano atatsutsana kwambiri,+ Petulo anaimirira, ndi kuwauza kuti: “Amuna inu, abale anga, mukudziwa bwino kuti m’masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu, kuti kudzera pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino ndi kukhulupirira.+ 8 Ndipo Mulungu, amene amadziwa zamumtima,+ anachitira umboni mwa kuwapatsa mzimu woyera,+ monga anachitiranso kwa ife. 9 Ndipo iye sanasiyanitse m’pang’ono pomwe pakati pa ife ndi iwo.+ Koma anayeretsa mitima yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.+ 10 Nanga tsopano n’chifukwa chiyani inu mukumuyesa Mulungu mwa kukanikizira goli pakhosi la ophunzira, goli+ limene makolo athu ngakhalenso ife sitinathe kulisenza?+ 11 Koma tsopano timakhulupirira kuti ife tidzapulumuka mwa kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye Yesu, mofanananso ndi anthu amenewa.”+
12 Pamenepo gulu lonselo linakhala chete, ndipo linayamba kumvetsera Baranaba ndi Paulo pamene anali kufotokoza zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo pakati pa anthu a mitundu ina.+ 13 Ataleka kulankhula, Yakobo anayankha kuti: “Amuna inu, abale anga, ndimvetsereni.+ 14 Sumeoni+ wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.+ 15 Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi mawu a m’Zolemba za aneneri. Mawuwo amati, 16 ‘Zimenezi zikadzatha ndidzabwerera ndi kumanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo ndi kuiimikanso.+ 17 Ndidzachita zimenezi kuti anthu otsalirawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu otchedwa ndi dzina langa, watero Yehova amene akuchita zinthu zimenezi,+ 18 zimene anatsimikiza kalekale kuti adzazichita.’+ 19 Choncho chigamulo changa n’chakuti, anthu amene akuchokera m’mitundu ina ndi kutembenukira kwa Mulungu, tisawavutitse.+ 20 Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,+ dama,*+ zopotola,+ ndi magazi.+ 21 Pakuti kuyambira kalekale, anthu akhala akulalikira mumzinda ndi mzinda mawu ochokera m’mabuku a Mose, chifukwa mabuku amenewa amawerengedwa mokweza m’masunagoge sabata lililonse.”+
22 Pamenepo atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwirizana zosankha amuna pakati pawo, kuti awatumize ku Antiokeya limodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Choncho anasankha Yudasi wotchedwa Barasaba,+ ndi Sila, amuna otsogolera pakati pa abale. 23 Chotero ndi manja awo analemba kuti:
“Ife abale anu atumwi pamodzi ndi akulu, tikulembera inu abale athu ochokera mwa anthu a mitundu ina, okhala ku Antiokeya,+ ku Siriya ndi ku Kilikiya:+ Landirani moni! 24 Tamva kuti ena ochokera pakati pathu akhala akulankhula mawu okusautsani,+ pofuna kupotoza maganizo anu, ngakhale kuti ife sitinawapatse malangizo aliwonse.+ 25 Pa chifukwa chimenechi, tonse tagwirizana chimodzi,+ ndipo tavomerezana kuti tisankhe amuna oti tiwatumize kwa inu limodzi ndi okondedwa athu, Baranaba ndi Paulo.+ 26 Amenewa ndi amuna omwe apereka miyoyo yawo chifukwa cha dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 27 Chotero tikutumiza Yudasi ndi Sila,+ kuti iwonso adzakufotokozereni zinthu zomwezi mwa mawu apakamwa.+ 28 Pakuti mzimu woyera+ pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera,+ kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi 29 kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano,+ magazi,+ zopotola,+ ndi dama.+ Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri,+ zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!”
30 Amuna amenewa atanyamuka, analowera ku Antiokeya. Kumeneko anasonkhanitsa khamu lonse la anthu ndi kuwapatsa kalatayo.+ 31 Ataiwerenga, anakondwera chifukwa cha mawu olimbikitsawo.+ 32 Ndiponso popeza kuti Yudasi ndi Sila anali aneneri,+ analimbikitsa abalewo ndi mawu ambiri ndipo anawapatsa mphamvu.+ 33 Atakhala kumeneko kanthawi, abalewo anawalola kubwerera mumtendere+ kwa amene anawatuma. 34* —— 35 Koma Paulo ndi Baranaba anatsalira ku Antiokeya.+ Ndipo iwo pamodzi ndi enanso ambiri anali kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova.+
36 Patapita masiku, Paulo anauza Baranaba kuti: “Tsopano, tiyeni tibwerere kumizinda yonse kumene tinafalitsa mawu a Yehova kuti tikachezere abale ndi kuwaona kuti ali bwanji.”+ 37 Chotero Baranaba anafunitsitsa kutenga Yohane, wotchedwa Maliko.+ 38 Koma Paulo anaona kuti n’kosayenera kumutenga kuti apite nawo. Anaona kuti n’kosayenera chifukwa ulendo wapita Yohane anawasiya ku Pamfuliya+ ndipo sanapite nawo ku ntchitoyi. 39 Pamenepo panabuka mkangano woopsa mpaka anapatukana. Baranaba+ anatenga Maliko ndipo anayenda ulendo wa pamadzi kulowera ku Kupuro.+ 40 Koma Paulo anasankha Sila,+ ndipo abale atamuikiza m’manja mwa Yehova kuti amusonyeze kukoma mtima kwakukulu, ananyamuka.+ 41 Iye anadzera ku Siriya ndi ku Kilikiya, ndipo anali kulimbitsa mipingo.+
16 Choncho Paulo anafika ku Debe ndiponso ku Lusitara.+ Kumeneko kunali wophunzira wina dzina lake Timoteyo,+ mwana wa mayi wachiyuda wokhulupirira, koma bambo ake anali Mgiriki. 2 Abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anamuchitira umboni wabwino. 3 Paulo anaonetsa kuti akufuna kumutenga pa ulendo wake. Chotero anamutenga ndi kum’dula+ chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko, pakuti onse anali kudziwa kuti bambo ake ndi Mgiriki. 4 Popitiriza ulendo wawo m’mizinda, anali kupatsa okhulupirira a kumeneko malamulo oyenera kuwatsatira, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula.+ 5 Choncho mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro+ ndipo chiwerengero chinapitiriza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.
6 Kenako iwo anapita ku Fulugiya ndiponso m’dziko la Galatiya,+ chifukwa mzimu woyera unawaletsa kulankhula mawu opatulika m’chigawo cha Asia. 7 Atafika ku Musiya anayesetsa kuti apite ku Bituniya,+ koma mzimu wa Yesu sunawalole. 8 Choncho analambalala Musiya ndi kukafika ku Torowa.+ 9 Ndiyeno usiku Paulo anaona masomphenya.+ Munthu wina wa ku Makedoniya anaimirira ndi kumupempha kuti: “Wolokerani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.” 10 Atangoona masomphenya amenewo, tinaganiza zopita ku Makedoniya.+ Tinali otsimikiza kuti Mulungu watiitana kuti tikalengeze uthenga wabwino kwa anthu akumeneko.
11 Chotero tinanyamuka ulendo wa panyanja kuchokera ku Torowa. Tinayenda molunjika mpaka ku Samatirake, koma tsiku lotsatira tinafika ku Neapoli. 12 Titachoka kumeneko tinafika ku Filipi,+ mzinda umene uli pansi pa ulamuliro wa Roma, umenenso ndi likulu la chigawo cha Makedoniya.+ Tinakhala mumzinda umenewu kwa masiku ndithu. 13 Tsiku la sabata tinatuluka pachipata n’kupita m’mbali mwa mtsinje, kumene tinali kuganiza kuti kuli malo opempherera. Ndiyeno tinakhala pansi ndi kuyamba kulankhula ndi amayi amene anali atasonkhana kumeneko. 14 Pamenepo panali mayi wina dzina lake Lidiya ndipo anali wolambira Mulungu. Iyeyu anali wochokera kumzinda wa Tiyatira+ ndipo anali wogulitsa nsalu ndi zovala zofiirira. Pamene anali kumvetsera, Yehova anatsegula kwambiri mtima wake+ kuti atchere khutu ku zimene Paulo anali kunena. 15 Tsopano iye ndi a m’banja lake atabatizidwa,+ anachonderera kuti: “Abale ngati inu mwaona kuti ndine wokhulupirika kwa Yehova, tiyeni mukalowe m’nyumba yanga ndi kukhala mmenemo.”+ Moti anatiumiriza ndithu kupita kwawo.+
16 Ndiyeno pamene tinali kupita kumalo opempherera, tinakumana ndi mtsikana wina wantchito wogwidwa ndi mzimu,+ chiwanda cholosera zam’tsogolo.+ Iye anali kupezera mabwana ake phindu lochuluka+ mwa kumachita zoloserazo. 17 Mtsikana ameneyu anali kumangotsatira Paulo ndi ife n’kumafuula kuti:+ “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wam’mwambamwamba, ndipo akulengeza njira ya chipulumutso kwa inu.” 18 Iye anakhala akuchita zimenezi kwa masiku ambiri. Potsirizira pake Paulo anatopa nazo+ ndipo anatembenuka n’kuuza mzimuwo kuti: “Ndikukulamula m’dzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa mtsikanayu.”+ Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.+
19 Koma mabwana ake aja ataona kuti chiyembekezo chawo chopeza phindu chatha,+ anagwira Paulo ndi Sila ndi kuwakokera mumsika, kubwalo la olamulira.+ 20 Atafika nawo kwa akuluakulu a boma, ananena kuti: “Anthu awa akusokoneza kwambiri+ mzinda wathu, chikhalirecho iwowa ndi Ayuda. 21 Ndipo akufalitsa miyambo+ imene kwa ife ndi yosaloleka kuitsatira kapena kuichita, popeza ndife Aroma.” 22 Pamenepo khamu la anthu linanyamuka pamodzi ndi kuukira atumwiwo. Ndipo akuluakulu a boma aja, anavula atumwiwo malaya awo akunja mochita kuwang’ambira ndi kulamula kuti awakwapule ndi zikoti.+ 23 Atawakwapula zikoti zambiri,+ anawaponya m’ndende ndi kulamula woyang’anira ndende kuti awasunge mosamala kwambiri.+ 24 Popeza kuti anamulamula zimenezi, iye anawaponya m’chipinda chamkati cha ndendeyo+ ndi kumanga mapazi awo m’matangadza.+
25 Koma chapakati pa usiku,+ Paulo ndi Sila anali kupemphera ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo,+ ndipo akaidi ena anali kuwamva. 26 Mwadzidzidzi panachitika chivomezi champhamvu, mpaka maziko a ndendeyo anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse zinatseguka, ndipo onse maunyolo awo anamasuka.+ 27 Woyang’anira ndende uja atadzuka ku tulo take ndi kuona kuti zitseko za ndende n’zotseguka, anasolola lupanga lake kuti adziphe,+ poganiza kuti akaidiwo athawa.+ 28 Pomwepo Paulo anafuula mokweza kuti: “Usadzivulaze,+ tonse tilipo!” 29 Pamenepo anapempha kuti amupatse nyale ndipo analumphira mkatimo. Akunjenjemera ndi mantha, anagwada+ pamaso pa Paulo ndi Sila. 30 Kenako anawatulutsa kunja n’kunena kuti: “Mabwana inu, ndichite chiyani+ kuti ndipulumuke?” 31 Iwo anati: “Khulupirira mwa Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka,+ limodzi ndi a m’nyumba yako.”+ 32 Ndipo analankhula mawu a Yehova kwa iye pamodzi ndi onse a m’nyumba yake.+ 33 Mu ola lomwelo la usiku, anawatenga ndi kuwatsuka zilonda zawo. Ndipo onse, iye ndi a m’banja lake, anabatizidwa+ mosataya nthawi. 34 Kenako anapita nawo kunyumba kwake ndi kuwaikira chakudya patebulo. Ndipo iye limodzi ndi onse a m’banja lake, anakondwera kwambiri chifukwa anakhulupirira Mulungu.
35 M’mawa mwake, akuluakulu a boma+ anatumiza asilikali kukanena kuti: “Amuna amenewo amasuleni.” 36 Choncho woyang’anira ndende uja anauza Paulo uthengawo, kuti: “Akuluakulu a boma atumiza anthu kudzanena kuti awirinu mumasulidwe. Choncho tulukani tsopano, ndipo mupite mu mtendere.” 37 Koma Paulo anawauza kuti: “Iwo atikwapula pamaso pa anthu ndi kutiponya m’ndende popanda kuzenga mlandu wathu, chikhalirecho ndife Aroma.+ Kodi tsopano akutitulutsa mseri? Ayi, zimenezo sizitheka! Abwere eniakewo adzatitulutse okha.” 38 Choncho asilikaliwo anauza akuluakulu a boma aja mawu amenewa. Pamenepo akuluakulu a bomawo anachita mantha atamva kuti anthuwo ndi Aroma.+ 39 Chotero anabwera ndi kuwachonderera, ndipo atawatulutsa anawapempha kuti achoke mumzindawo. 40 Koma iwo anatuluka m’ndendemo n’kupita kunyumba kwa Lidiya. Ataona abale, anawalimbikitsa+ kenako ananyamuka n’kumapita.
17 Iwo tsopano anayenda kudutsa ku Amfipoli ndi ku Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika,+ kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2 Choncho mwachizolowezi chake,+ Paulo analowa m’sunagogemo, ndipo kwa masabata atatu anakambirana nawo mfundo za m’Malemba.+ 3 Iye anali kufotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti kunali koyenera kuti Khristu avutike+ ndi kuuka kwa akufa.+ Anali kunena kuti: “Yesu amene ndikumulalikira kwa inu, ndiye Khristu.”+ 4 Zotsatira zake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira+ ndipo anagwirizana ndi Paulo ndi Sila.+ Ndipo khamu lalikulu la Agiriki opembedza Mulungu, ndi amayi ambiri olemekezeka anachitanso chimodzimodzi.
5 Koma Ayuda anachita nsanje,+ ndipo anatengana ndi anthu ena oipa, anthu osowa chochita amene anali kungokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa ndi kuyambitsa chipolowe mumzindamo.+ Kenako anakhamukira kunyumba ya Yasoni,+ kukafuna atumwiwo kuti awatulutsire ku gulu lachipolowelo. 6 Atalephera kuwapeza, anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: “Anthu awa amene abweretsa mavuto+ padziko lapansi kumene kuli anthu, tsopano akupezekanso kuno, 7 ndipo Yasoni anawalandira bwino. Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo+ a Kaisara. Akunena kuti eti kulinso mfumu ina+ dzina lake Yesu.” 8 Ndi mawu amenewa, iwo anautsa mkwiyo wa khamu la anthu lija ndi olamulira a mzindawo. 9 Pamenepo olamulira a mzindawo analipiritsa Yasoni ndi enawo ndalama, kenako anawamasula.
10 Kutangoda,+ abale anatulutsa Paulo ndi Sila ndi kuwatumiza ku Bereya. Iwo atafika kumeneko, analowa m’sunagoge wa Ayuda. 11 Koma anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzira kuposa a ku Tesalonika aja. Iwowa analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku anali kufufuza+ Malemba+ mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.+ 12 Chotero ambiri a iwo anakhala okhulupirira, chimodzimodzinso akazi ndi amuna ambiri otchuka+ achigiriki. 13 Koma Ayuda ochokera ku Tesalonika atamva kuti Paulo akufalitsanso mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko kukayambitsa chipolowe+ ndi kuchititsa anthuwo kukwiyira+ atumwiwo. 14 Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo kuti apite kunyanja.+ Koma Sila ndi Timoteyo anatsalira kumeneko. 15 Ndipo anthu amene anaperekeza Paulo anakamufikitsa ku Atene. Koma anabwerera atatumidwa kuti akauze Sila ndi Timoteyo+ kuti amutsatire msanga.
16 Pamene Paulo anali kuwayembekezera ku Atene, mtima unamuwawa kwambiri+ poona kuti mumzindawo mwadzaza mafano. 17 Choncho ali m’sunagoge anayamba kukambirana ndi Ayuda+ ndi anthu ena opembedza Mulungu. Ndipo tsiku ndi tsiku analinso kukambirana ndi anthu amene anali kuwapeza pamsika.+ 18 Koma ena anzeru za dziko, Aepikureya ndi Asitoiki+ anayamba kutsutsana naye. Ndipo ena anali kunena kuti: “Kodi nayenso wobwetuka uyu akufuna kunena chiyani?”+ Enanso anali kunena kuti: “Akuoneka kuti ndi wofalitsa za milungu yachilendo.” Ananena zimenezi chifukwa chakuti Paulo anali kulengeza uthenga wabwino wa Yesu ndi za kuuka kwa akufa.+ 19 Choncho anamugwira n’kupita naye kubwalo la Areopagi, ndi kunena kuti: “Kodi tingadziweko za chiphunzitso chatsopanochi+ chimene iwe ukuphunzitsa? 20 Chifukwatu zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo m’makutu mwathu. Choncho tikufuna tidziwe tanthauzo la zimenezi.”+ 21 Ndipotu nzika zonse za mu Atene ndi alendo ogonera kumeneko, anali kuthera nthawi yawo yonse yopuma akufotokoza kapena kumvetsera nkhani yatsopano. 22 Tsopano Paulo anaimirira pakati pa bwalo la Areopagi+ ndi kunena kuti:
“Amuna inu a mu Atene, ndaona kuti pa zinthu zonse mumaopa kwambiri milungu+ kuposa mmene ena amachitira. 23 Mwachitsanzo, pamene ndinali kudutsa ndi kuyang’anitsitsa zinthu zimene mumalambira, ndapezanso guwa lansembe lolembedwa kuti ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Chotero ine ndikulalikira kwa inu za Mulungu wosadziwika amene mukumulambirayo. 24 Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.+ Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.+ 25 Komanso satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu,+ chifukwa ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo,+ mpweya,+ ndi zinthu zonse. 26 Ndipo kuchokera mwa munthu mmodzi+ anapanga mtundu wonse wa anthu,+ kuti akhale padziko lonse lapansi.+ Iye anakhazikitsa nthawi zoikidwiratu+ komanso anaika malire achikhalire a malo oti anthu azikhala.+ 27 Anachita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu,+ amufufuzefufuze ndi kumupezadi,+ ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28 Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo,+ monga mmene andakatulo+ ena pakati panu anenera kuti, ‘Pakuti ndife mbadwa zake.’
29 “Popeza kuti ndife mbadwa za Mulungu,+ tisaganize kuti Mulunguyo+ ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu.+ 30 Zoona, Mulungu analekerera nthawi ya kusadziwa koteroko,+ koma tsopano akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape.+ 31 Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika. Ndipo wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa+ kwa akufa.”
32 Ndiyeno anthuwo atamva za kuuka kwa akufa, ena anayamba kuseka monyodola,+ pamene ena anati: “Chabwino, udzatiuzenso zimenezi nthawi ina.” 33 Choncho Paulo anachoka pakati pawo. 34 Koma anthu ena anakhala kumbali yake ndipo anakhala otsatira a Yesu. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, woweruza m’bwalo la Areopagi,+ mayi wina dzina lake Damarisi ndi ena ambiri.
18 Zimenezi zitatha, Paulo anachoka ku Atene n’kupita ku Korinto. 2 Kumeneko anapeza Myuda wina dzina lake Akula,+ mbadwa ya ku Ponto. Iyeyu pamodzi ndi mkazi wake Purisikila, anali atafika chaposachedwa kuchokera ku Italiya,+ chifukwa Kalaudiyo+ anali atalamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Choncho Paulo anapita kwa iwo. 3 Ndipo popeza kuti ntchito yawo inali imodzi, anakhala kunyumba kwawoko. Iwo ankagwira ntchito pamodzi,+ pakuti onse anali amisiri opanga mahema. 4 Komabe Paulo anali kukamba nkhani m’sunagoge+ sabata lililonse, ndipo anali kukopa Ayuda ndi Agiriki.
5 Tsopano Sila+ ndi Timoteyo+ atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu. Iye anali kuchitira umboni kwa Ayuda ndi kuwatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.+ 6 Koma iwo atapitiriza kumutsutsa ndi kulankhula monyoza,+ iye anakutumula zovala zake+ ndi kuwauza kuti: “Magazi anu+ akhale pamitu panu. Ine ndilibe mlandu.+ Kuyambira tsopano ndizipita kwa anthu a mitundu ina.”+ 7 Zitatero, iye anachoka pamenepo ndi kupita kunyumba ya munthu wina dzina lake Titiyo Yusito. Iyeyu anali wolambira Mulungu, ndipo nyumba yake inali moyandikana ndi sunagoge. 8 Kirisipo,+ mtsogoleri wa sunagoge, anakhala wokhulupirira mwa Ambuye, pamodzi ndi onse a m’banja lake. Ndipo Akorinto ambiri amene anamva uthenga wabwino anayamba kukhulupirira ndi kubatizidwa. 9 Komanso usiku, Ambuye anauza Paulo+ m’masomphenya kuti: “Usaope, pitiriza kulankhula. Usakhale chete, 10 chifukwa ine ndili nawe.+ Palibe munthu amene adzakukhudze ndi kukuvulaza, pakuti ndili ndi anthu ambiri mumzinda uno.” 11 Choncho anakhazikika kumeneko chaka ndi miyezi 6, akuwaphunzitsa mawu a Mulungu.
12 Tsopano pamene Galiyo anali bwanamkubwa+ wa Akaya, Ayuda ananyamuka mogwirizana ndi kuukira Paulo, ndipo anamutengera kumpando woweruzira milandu.+ 13 Kumeneko iwo anati: “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu m’njira yosemphana ndi chilamulo.”+ 14 Koma pamene Paulo ankati azitsegula pakamwa, Galiyo anauza Ayudawo kuti: “Ayuda inu, chikanakhala cholakwa china, kapena pakanachitika chinachake choipa, ndithu ndikanaleza mtima ndi kukumverani. 15 Koma ngati nkhani yake ili yokhudza mikangano pa mawu, mayina+ ndi chilamulo+ chanu, zimenezo muthane nazo nokha. Ine sindikufuna kuti ndikhale woweruza nkhani zoterezi.” 16 Atatero anawapitikitsa kumpando woweruzira milanduwo. 17 Zitatero, onse anagwira Sositene,+ mtsogoleri wa sunagoge ndi kuyamba kumumenya pafupi ndi mpando woweruzira milanduwo. Koma Galiyo sanasamale zimenezo ngakhale pang’ono.
18 Koma Paulo atakhala kumeneko masiku ndithu, anatsanzikana ndi abalewo ndipo anapitiriza ulendo wake wa pamadzi kulowera ku Siriya. Pa ulendowu anatsagana ndi Purisikila ndi Akula. Paulo anameta tsitsi lake+ ku Kenkereya+ chifukwa cha lonjezo limene anachita. 19 Choncho onse anafika ku Efeso, ndipo anzakewo anawasiya kumeneko. Koma iye yekha analowa m’sunagoge+ ndi kuyamba kukambirana ndi Ayuda. 20 Ngakhale kuti anamupempha mobwerezabwereza kuti akhale nawo kwa nthawi yotalikirapo, iye sanalole. 21 M’malomwake, anatsanzikana+ nawo ndi kuwauza kuti: “Yehova akalola ndidzabweranso kudzakuonani.”+ Choncho ananyamuka ku Efeso ulendo wa panyanja 22 ndipo anafika ku Kaisareya. Kenako anapita* kukapereka moni ku mpingo, ndipo pambuyo pake anapita ku Antiokeya.
23 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, ananyamuka ndi kuyenda malo osiyanasiyana m’chigawo cha Galatiya+ ndi Fulugiya,+ ndipo anali kulimbikitsa+ ophunzira onse.
24 Tsopano Myuda wina dzina lake Apolo,+ mbadwa ya ku Alekizandiriya, amene anali ndi mphatso ya kulankhula, anafika ku Efeso. Iyeyu analinso kuwadziwa bwino Malemba.+ 25 Mwamuna ameneyu analangizidwa njira ya Yehova ndi mawu a pakamwa. Ndiyeno popeza kuti anali wodzipereka kwambiri chifukwa chakuti anali ndi mzimu woyera,+ anali kulankhula ndi kuphunzitsa molondola za Yesu. Koma anali kudziwa za ubatizo+ wa Yohane wokha basi. 26 Mwamuna ameneyu anayamba kulankhula molimba mtima musunagoge. Tsopano Purisikila ndi Akula+ atamumvetsera, anamutenga ndi kumufotokozera njira ya Mulungu molondola. 27 Ndiponso, popeza kuti anali wofunitsitsa kupita ku Akaya, abalewo analembera ophunzira kumeneko. Anawalimbikitsa kuti amulandire ndi manja awiri. Choncho iye atafika kumeneko, anathandiza kwambiri+ anthu amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+ 28 Pakuti mwamphamvu, iye anawatsimikizira Ayuda poyera kuti anali olakwa, ndipo anasonyeza mwa Malemba+ kuti Yesu ndiyedi Khristu.+
19 Nthawi inayake, Apolo+ ali ku Korinto, Paulo anadzera kumadera a kumtunda mpaka anafika ku Efeso.+ Kumeneko anapezako ophunzira ena, 2 ndipo anawafunsa kuti: “Kodi munalandira mzimu woyera+ mutakhala okhulupirira?” Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu sitinamvepo kuti kuli mzimu woyera.”+ 3 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga munabatizidwa ubatizo wamtundu wanji?” Iwo anayankha kuti: “Tinabatizidwa ubatizo wa Yohane.”+ 4 Pamenepo Paulo anati: “Yohane anabatiza anthu ubatizo umene unali chizindikiro chakuti munthu walapa.+ Anali kuuza anthu kuti akhulupirire amene anali kubwera m’mbuyo mwake,+ kutanthauza Yesu.” 5 Atamva zimenezi, anthuwo anabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.+ 6 Ndiyeno Paulo atawaika manja,+ mzimu woyera unafika pa iwo, ndipo anayamba kulankhula malilime ndi kunenera.+ 7 Onse pamodzi anali amuna pafupifupi 12.
8 Kwa miyezi itatu, anali kupita kusunagoge+ kumene anali kulankhula molimba mtima. Kumeneko anali kukamba nkhani ndi kuwafotokozera mfundo zokhutiritsa zokhudza ufumu+ wa Mulungu. 9 Koma ena anapitiriza kuumitsa mitima yawo osakhulupirira,+ ndipo anali kunena zonyoza Njirayo+ pamaso pa khamu la anthu. Choncho iye anawachokera+ n’kuchotsanso ophunzirawo pakati pawo.+ Ndipo tsiku ndi tsiku anali kukamba nkhani m’holo pasukulu ya Turano. 10 Izi zinachitika kwa zaka ziwiri,+ moti onse okhala m’chigawo cha Asia,+ Ayuda ndi Agiriki omwe, anamva mawu a Ambuye.
11 Mulungu anapitiriza kuchita ntchito zamphamvu zodabwitsa kudzera mwa Paulo.+ 12 Moti anthu anali kutenga ngakhale mipango yopukutira thukuta ndi maepuloni amene akhudza thupi la Paulo n’kupita nazo kwa odwala,+ ndipo matenda awo anali kutheratu. Mizimu yoipa nayonso inali kutuluka.+ 13 Koma Ayuda ena oyendayenda amene anali kutulutsa ziwanda,+ anayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu+ pofuna kuchiritsa anthu okhala ndi mizimu yoipa. Anali kunena kuti: “Ndikukulamulani+ mwa Yesu amene Paulo akumulalikira.” 14 Choncho panali ana aamuna 7 a Sikeva, wansembe wamkulu wachiyuda, amene anali kuchita zimenezi. 15 Koma mzimu woipa poyankha unawauza kuti: “Ine Yesu ndikumudziwa,+ ndipo Paulo ndikumudziwanso bwino.+ Nanga inuyo ndinu ndani?” 16 Kenako, munthu amene anali ndi mzimu woipa uja anawalumphira.+ Analimbana nawo mmodzimmodzi ndi kuwagonjetsa onsewo, mwakuti anatuluka m’nyumbamo ndi kuthawa ali maliseche komanso atavulala. 17 Izi zinadziwika kwa onse, Ayuda ndi Agiriki amene anali kukhala ku Efeso. Chotero onse anagwidwa ndi mantha,+ ndipo dzina la Ambuye Yesu linapitirira kulemekezedwa.+ 18 Anthu ambiri amene anakhala okhulupirira anali kubwera kudzaulula machimo+ awo ndi kufotokoza poyera zoipa zimene anali kuchita. 19 Ndithudi, ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga+ anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000. 20 Choncho mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndi kugonjetsa zopinga zambiri.+
21 Tsopano izi zitatha, Paulo anatsimikiza mumtima mwake kupita ku Yerusalemu,+ kudzera ku Makedoniya+ ndi ku Akaya. Iye anati: “Ndikakafika kumeneko, ndiyeneranso kukaona ku Roma.”+ 22 Choncho ku Makedoniya anatumizako awiri mwa anthu amene anali kumutumikira, omwe ndi Timoteyo+ ndi Erasito.+ Koma iye anatsalira m’chigawo cha Asia kwa kanthawi ndithu.
23 Pa nthawi yomweyo panabuka chisokonezo chachikulu+ chokhudzana ndi Njirayo.+ 24 Panali munthu wina wosula siliva dzina lake Demetiriyo. Amisiri anali kupeza phindu lochuluka chifukwa cha ntchito yake yopanga tiakachisi tasiliva ta Atemi.+ 25 Choncho Demetiriyo anasonkhanitsa amisiriwo, limodzi ndi anthu ogwira ntchito yokhudzana ndi zinthu zimenezo.+ Ndiyeno anawauza kuti: “Amuna inu, mukudziwa bwino kuti chuma chathu chimachokera m’ntchito imeneyi.+ 26 Tsopano mukuona ndipo mukumva za Paulo ameneyu, kuti si mu Efeso+ mokha muno mmene wakopa anthu ambirimbiri ndi kuwapatutsira ku chikhulupiriro china. Wachita zimenezi pafupifupi m’chigawo chonse cha Asia. Iye akumanena kuti milungu yopangidwa ndi manja+ si milungu ayi. 27 Ndipo chimene chikuopsa kwambiri si kunyozeka kwa ntchito yathu kokha ayi, komanso kachisi wa mulungu wamkulu wamkazi Atemi+ adzayesedwa wopanda pake. Ndipotu aliyense m’chigawo chonse cha Asia komanso padziko lapansi kumene kuli anthu amalemekeza Atemi. Koma chifukwa cha zimene Paulo akunena ulemerero umenewo watsala pang’ono kuti utheretu.” 28 Atamva zimenezi anthuwo anakwiya kwambiri ndi kuyamba kufuula kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!”
29 Pamenepo mumzindawo munadzaza chisokonezo, ndipo onse pamodzi anathamangira m’bwalo la masewera, atagwira Gayo ndi Arisitako n’kuwakokera m’bwalomo. Gayo ndi Arisitako+ anali anzake a Paulo amene anali kuyenda naye ndipo kwawo kunali ku Makedoniya. 30 Choncho Paulo anafuna kulowa mkati mwa khamu la anthulo, koma ophunzira sanamulole. 31 Ngakhalenso ena oyang’anira zikondwerero ndi masewera, amene anali anzake anamutumizira uthenga womuchonderera kuti asaike moyo wake pachiswe mwa kulowa m’bwalo la maseweralo. 32 Kunena zoona, khamu lonse linali pa chipwirikiti, ena anali kufuula zina enanso zina.+ Mwakuti ambiri a iwo sanadziwe n’komwe chifukwa chimene anasonkhanira pamodzi. 33 Choncho iwo anatulutsa Alekizanda m’khamulo, ndipo Ayuda anamukankhira kutsogolo. Kenako Alekizanda anatambasula dzanja lake kuti alankhule podziteteza kwa anthuwo. 34 Koma iwo atazindikira kuti iye ndi Myuda, onse pamodzi anafuula kwa maola pafupifupi awiri kuti: “Wamkulu+ ndi Atemi mulungu wa Aefeso!”
35 Pamapeto pake, woyang’anira mzinda atakhalitsa chete+ khamu la anthulo, anati: “Anthu inu a mu Efeso, alipo kodi munthu amene sadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo woyang’anira kachisi wa Atemi wamkulu ndi chifaniziro chimene chinagwa kuchokera kumwamba? 36 Chotero, popeza kuti palibe amene angatsutse zimenezi, muyenera kudekha, musachite zinthu mopupuluma.+ 37 Pakuti mwabweretsa anthu awa amene si akuba mu akachisi kapena onyoza mulungu wathu wamkaziyo. 38 Choncho ngati Demetiriyo+ ndi amisiri ali nawowa akuimba mlandu munthu, pamakhala masiku a milandu+ ndipo abwanamkubwa+ alipo. Akasumirane kumeneko. 39 Koma ngati mukufuna zina zoposa pamenepa, zimenezo ziyenera kukagamulidwa pabwalo lovomerezeka. 40 Chifukwa kunena zoona, kuopsa kwa zimene zachitika lerozi n’kwakuti angathe kutiimba nazo mlandu woukira boma. Palibiretu chifukwa chomveka chimene tingapereke pa chipolowe chimene chachitikachi.” 41 Atanena zimenezi,+ anauza osonkhanawo kuti achoke pamalowo.+
20 Chipolowe chija chitatha, Paulo anaitanitsa ophunzira. Atawalimbikitsa ndi kutsanzikana nawo,+ ananyamuka ulendo wopita ku Makedoniya.+ 2 Iye anayendayenda m’madera akumeneko ndi kulimbikitsa ophunzira ndi mawu ambiri,+ kenako anafika ku Girisi. 3 Atakhala kumeneko miyezi itatu, anaganiza zobwerera ku Makedoniya, chifukwa chakuti Ayuda anamukonzera chiwembu.+ Chiwembuchi anachikonza Paulo atangotsala pang’ono kuyamba ulendo wa pamadzi wopita ku Siriya. 4 Amene anatsagana naye pa ulendowu anali Sopaturo+ mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako+ ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe, ndi Timoteyo,+ koma ochokera m’chigawo cha Asia anali Tukiko+ ndi Terofimo.+ 5 Iwowa anatsogola ndipo anali kutiyembekezera ku Torowa.+ 6 Koma tinayamba ulendo wa panyanja ku Filipi masiku a mkate wopanda chofufumitsa atatha.+ Ndipo tinawapeza ku Torowa+ patapita masiku asanu. Kumeneko tinakhalako masiku 7.
7 Pa tsiku loyamba+ la mlungu, titasonkhana pamodzi kuti tidye chakudya, Paulo anayamba kuwakambira nkhani, chifukwa anali kunyamuka m’mawa wake. Ndipo anatenga nthawi yaitali akulankhula mpaka pakati pa usiku. 8 M’chipinda cham’mwamba+ mmene tinasonkhanamo, munali nyale zambiri ndithu. 9 Paulo ali mkati mokamba nkhani, mnyamata wina dzina lake Utiko amene anakhala pawindo, anagona tulo tofa nato. Ali m’tulo choncho, anagwa pansi kuchokera panyumba yachitatu yosanja, ndipo anamupeza atafa. 10 Koma Paulo anatsika pansi, ndipo anadziponya pa iye+ ndi kumukumbatira. Kenako ananena kuti: “Khalani chete, pakuti ali moyo tsopano.”+ 11 Atatero Paulo anakweranso m’chipinda cham’mwamba chija. Kenako ananyemanyema mkate n’kuyamba kudya, ndipo atakambirana kwa nthawi yaitali mpaka m’mawa, ananyamuka n’kumapita. 12 Koma iwo anatenga mnyamata uja ali wamoyo, ndipo anatonthozedwa kwambiri.
13 Tsopano ife tinatsogola kukakwera ngalawa n’kuyamba ulendo wopita ku Aso, kumene tinali kukatenga Paulo pangalawa. Iye anatilangiza kuti titsogole, chifukwa anafuna kuyenda wapansi. 14 Choncho atatipeza ku Aso, tinamukweza m’ngalawa ndi kupita ku Mitilene. 15 M’mawa wake titachoka kumeneko, tinafika pamalo oyang’anana ndi Kiyo. Koma tsiku lotsatira tinaima kwa kanthawi ku Samo, ndipo m’mawa wake tinafika ku Mileto. 16 Paulo anaganiza zongolambalala Efeso,+ kuti asataye nthawi m’chigawo cha Asia. Anachita zimenezi chifukwa anali kufulumira kuti ngati n’kotheka, akakhale ali ku Yerusalemu+ pa tsiku la chikondwerero cha Pentekosite.
17 Komabe ali ku Mileto anatuma mthenga ku Efeso kuti akaitane akulu+ a mpingo. 18 Akuluwo atafika, iye anawauza kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinali kukhalira nanu nthawi zonse kuchokera tsiku loyamba limene ndinaponda m’chigawo cha Asia.+ 19 Ndinali kutumikira+ Ambuye monga kapolo, modzichepetsa kwambiri,+ ndi misozi komanso ndi mayesero amene anandigwera chifukwa cha ziwembu+ za Ayuda. 20 Komatu sindinakubisireni chilichonse chopindulitsa, ndipo sindinaleke kukuphunzitsani+ poyera komanso kunyumba+ ndi nyumba. 21 Koma ndachitira umboni mokwanira+ kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape+ ndi kutembenukira kwa Mulungu, komanso kuti akhale ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu. 22 Ndipo tsopano, popeza kuti mzimu wandikakamiza,+ ndikupita ku Yerusalemu, ngakhale kuti sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko. 23 Chimodzi chokha chimene ndikudziwa n’chakuti mumzinda ndi mzinda, mzimu woyera+ wandichitira umboni mobwerezabwereza kuti maunyolo ndi masautso akundiyembekezera.+ 24 Komabe, moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ayi.+ Chimene ndikungofuna n’chakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu,+ komanso kuti ndimalize utumiki+ umene ndinalandira+ kwa Ambuye Yesu basi. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+
25 “Ndipo tamverani tsopano! Ndikudziwa kuti nonsenu amene ndinakulalikirani za ufumu, nkhope yanga simudzaionanso. 26 Choncho mukhale mboni lero, kuti ine ndine woyera pa mlandu wa magazi+ a anthu onse. 27 Pakuti sindinakubisireni kanthu, koma ndinakuuzani chifuniro+ chonse cha Mulungu. 28 Mukhale tcheru ndi kuyang’anira+ gulu lonse la nkhosa,+ limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira,+ kuti muwete mpingo wa Mulungu,+ umene anaugula ndi magazi+ a Mwana wake weniweni. 29 Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu+ yopondereza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. 30 Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka+ kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.+
31 “Choncho khalani maso, ndipo kumbukirani kuti kwa zaka zitatu,+ usana ndi usiku, sindinaleke kuchenjeza+ aliyense wa inu ndi misozi. 32 Koma tsopano ndikukuperekani kwa Mulungu+ ndi ku mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu. Mawu amenewo angakulimbikitseni+ ndi kukupatsani cholowa pakati pa oyeretsedwa onse.+ 33 Sindinasirire mwa nsanje siliva, golide kapena chovala cha munthu.+ 34 Inunso mukudziwa bwino kuti manja awa anagwira ntchito kuti ndipeze zosowa zanga+ ndi za amene ali nane. 35 M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi,+ muthandize ofookawo,+ ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka+ kuposa kulandira.’”
36 Atanena zimenezi, anagwada+ nawo pansi onsewo ndi kupemphera. 37 Pamenepo onse analira kwambiri, ndipo anakumbatira+ Paulo ndi kumupsompsona mwachikondi.+ 38 Iwo anamva chisoni kwambiri, makamaka chifukwa cha mawu amene iye ananena akuti sadzaonanso nkhope yake.+ Kenako anamuperekeza+ kukakwera ngalawa.
21 Tsopano titadzikakamiza kulekana nawo n’kuyamba ulendo wathu wa panyanja, tinayenda molunjika mpaka kufika ku Ko. Koma tsiku lotsatira tinafika ku Rode, ndipo titachoka kumeneko tinakafika ku Patara. 2 Kumeneko tinapeza ngalawa imene inali kuwolokera ku Foinike, ndipo tinakwera ndi kunyamuka. 3 Chilumba cha Kupuro+ chitayamba kuonekera, tinachisiya kumanzere ndi kupitiriza ulendo wathu kulowera ku Siriya.+ Tinaima ku Turo, chifukwa kumeneko ngalawa inafunika kutsitsa katundu.+ 4 Titafufuza tinapeza ophunzira ndi kukhala nawo kumeneko masiku 7. Koma mouziridwa ndi mzimu,+ iwo anauza Paulo mobwerezabwereza kuti asakaponde mu Yerusalemu. 5 Choncho titatsiriza masikuwo, tinanyamuka kuti tipitirize ulendo wathu. Ndipo abale onse, pamodzi ndi amayi ndi ana, anatiperekeza mpaka kunja kwa mzindawo. Kumeneko tinagwada+ pagombe ndi kupemphera 6 n’kutsanzikana.+ Kenako ife tinakwera ngalawa ndipo iwo anabwerera kunyumba zawo.
7 Choncho tinanyamuka ku Turo pangalawa ndipo tinafika ku Tolemayi. Kumeneko tinalonjerana ndi abale ndi kukhala nawo tsiku limodzi. 8 M’mawa mwake tinanyamuka ndi kukafika ku Kaisareya.+ Kumeneko tinakalowa m’nyumba ya mlaliki* Filipo. Iyeyu anali mmodzi wa amuna 7 a mbiri yabwino aja,+ ndipo tinakhala naye. 9 Mwamuna ameneyu anali ndi ana aakazi anayi, anamwali, amene anali kunenera.+ 10 Koma titakhala masiku ndithu, mneneri wina dzina lake Agabo+ anafika kumeneko kuchokera ku Yudeya. 11 Iye anafika kwa ife ndi kutenga lamba wa Paulo. Kenako anadzimanga mapazi ndi manja ndi kunena kuti: “Mzimu woyera wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga+ chonchi ku Yerusalemu ndi kumupereka+ m’manja mwa anthu a mitundu ina.’” 12 Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu akumeneko, tinayamba kuchonderera Paulo kuti asapite+ ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anayankha kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira+ ndi kunditayitsa mtima?+ Dziwani kuti ine ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kukafa+ ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” 14 Titalephera kumusintha maganizo, tinangovomereza ndi kunena kuti: “Chifuniro+ cha Yehova chichitike.”
15 Masiku amenewa atapita, tinakonzekera ulendo ndipo tinanyamuka kulowera ku Yerusalemu.+ 16 Koma ophunzira ena a ku Kaisareya+ ananyamuka nafe, kuti atiperekeze kunyumba ya munthu wina kuti tikafikire kumeneko. Munthu ameneyu dzina lake linali Mnaso wa ku Kupuro, ndipo anali mmodzi wa ophunzira oyambirira. 17 Titafika ku Yerusalemu,+ abale anatilandira mokondwa.+ 18 Koma tsiku lotsatira, Paulo anapita nafe kwa Yakobo,+ ndipo akulu onse anali komweko. 19 Paulo anawalonjera ndi kuyamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane+ zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.+
20 Iwo atamva zimenezi anayamba kutamanda Mulungu, ndipo anamuuza kuti: “M’bale, kodi ukuona kuchuluka kwa okhulupirira amene ali pakati pa Ayuda? Ndipo onsewa ndi odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo.+ 21 Komatu iwo amva mphekesera zakuti iwe wakhala ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti apandukire Chilamulo cha Mose.+ Akuti ukuwauza kuti asamachite mdulidwe+ wa ana awo kapena kutsatira miyambo imene takhala tikuitsatira kuyambira kale. 22 Tsopano tichite chiyani pamenepa? Sitikukayikira kuti iwo adzamva ndithu kuti iwe wafika. 23 Choncho uchite zimene tikuuze pano: Tili ndi amuna anayi amene anachita lumbiro. 24 Utenge amuna amenewa+ ndipo ukachite mwambo wa kudziyeretsa pamodzi ndi iwo. Uwalipirire zonse zofunika,+ kuti amete tsitsi lawo.+ Ukatero, aliyense adzadziwa kuti mphekesera zimene anamva za iwe ndi nkhambakamwa chabe. Adzaona kuti ukuchita zinthu motsatira dongosolo, komanso kuti umasunga Chilamulo.+ 25 Koma kwa okhulupirira ochokera mwa anthu a mitundu inawo, tinawatumizira chigamulo chathu chakuti apewe zoperekedwa nsembe kwa mafano+ komanso magazi,+ zopotola,+ ndi dama.”+
26 Choncho Paulo anatenga amunawo tsiku lotsatira ndi kukachita mwambo wa kudziyeretsa pamodzi ndi iwo.+ Kenako analowa m’kachisi, kukanena pamene masiku awo a mwambo wa kudziyeretsa adzathere,+ ndi pamene aliyense wa iwo adzamuperekere nsembe.+
27 Ali pafupi kutsiriza masiku 7,+ Ayuda ochokera ku Asia anaona Paulo ali m’kachisi. Chotero anayambitsa chisokonezo+ m’khamu lonse la anthu ndipo anamugwira. 28 Iwo anali kufuula kuti: “Inu Aisiraeli, tithandizeni! Munthu amene akuphunzitsa zotsutsana ndi anthu a mtundu wathu kulikonse ndi ameneyu.+ Iyeyu akuphunzitsa zotsutsana ndi Chilamulo komanso malo ano. Kuwonjezera pamenepo, inu mukudziwa kuti anatenga Agiriki n’kudzawalowetsa m’kachisi ndipo waipitsa malo oyera ano.”+ 29 Iwo ananena zimenezi chifukwa tsiku lina anaona Terofimo+ wa ku Efeso ali naye limodzi mumzindawo. Atawaona anaganiza kuti Paulo analowetsa Terofimo m’kachisi. 30 Chotero munali chisokonezo mumzinda wonsewo, ndipo anthu anali balalabalala+ kuthamangira kukachisiko. Kenako anagwira Paulo ndi kumukokera kunja kwa kachisi.+ Nthawi yomweyo zitseko zinatsekedwa. 31 Ndipo pamene anali kufuna kumupha, uthenga unafika kwa mtsogoleri wa gulu la asilikali kuti mu Yerusalemu monse muli chisokonezo.+ 32 Mwamsanga, iye anatenga asilikali ndi akapitawo awo ndi kuthamangira kumeneko.+ Anthuwo ataona mkulu wa asilikali+ uja pamodzi ndi asilikali akewo, analeka kumenya Paulo.
33 Pamenepo mkulu wa asilikali uja anafika pafupi ndi kumugwira ndipo analamula kuti amumange ndi maunyolo awiri.+ Ndiyeno anafunsa za iye kuti anali ndani ndiponso zimene anachita. 34 Koma ena m’khamulo anayamba kufuula zinthu zina, enanso zina.+ Choncho, atalephera kutolapo mfundo yeniyeni chifukwa cha phokoso, analamula kuti apite naye kumpanda wa asilikali.+ 35 Ndiyeno atafika pamasitepe, asilikaliwo anachita kumunyamula chifukwa chakuti khamulo linali kuchita chiwawa. 36 Khamu la anthu linali kuwatsatira, likufuula kuti: “Aphedwe ameneyo!”+
37 Koma atatsala pang’ono kulowa naye kumpanda wa asilikali, Paulo anauza mkulu wa asilikali kuti: “Mungandilole kodi kulankhula nanu pang’ono?” Iye anati: “Kodi umalankhula Chigiriki? 38 Kodi si iwe Mwiguputo uja amene masiku apitawo unayambitsa chipolowe choukira boma+ ndi kutsogolera zigawenga 4,000 kupita nazo m’chipululu?” 39 Pamenepo Paulo ananena kuti: “Inetu ndine Myuda+ wa ku Tariso,+ ku Kilikiya, nzika ya mzinda wotchuka. Chonde ndikukupemphani, kuti mundilole ndilankhule kwa anthuwa.” 40 Atamulola, Paulo anaimirira pamasitepe ndi kukwezera anthuwo dzanja.+ Onse atakhala phee, analankhula nawo m’Chiheberi,+ kuti:
22 “Amuna inu, abale anga+ ndi abambo anga, tsopano mvetserani mawu anga odziteteza+ pamaso panu.” 2 (Atamva kuti akulankhula nawo m’Chiheberi,+ onse anangoti zii osanena kanthu, ndipo iye anati:) 3 “Inetu ndine Myuda,+ wobadwira ku Tariso wa ku Kilikiya,+ koma ndinaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli+ mumzinda womwe uno. Anandiphunzitsa kutsatira Chilamulo cha makolo athu mokhwimitsa zinthu kwambiri.+ Ndipo ndinali wodzipereka+ potumikira Mulungu monga mmene nonsenu mulili lero. 4 Ndinazunza otsatira Njira imeneyi mpaka imfa.+ Ndinali kumanga amuna ndi akazi ndi kuwapereka kundende.+ 5 Ndipotu mkulu wa ansembe ndi bungwe lonse la akulu+ angandichitire umboni. Kwa amenewa n’kumene ndinapezanso makalata+ opita kwa abale ku Damasiko. Ndinanyamuka kuti ndikagwire okhala kumeneko ndi kuwabweretsa ku Yerusalemu ali omangidwa kuti adzapatsidwe chilango.
6 “Koma ndili m’njira, ndikuyandikira ku Damasiko, dzuwa lili pamutu, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunangoti ngwee! kuzungulira pamene ine ndinali.+ 7 Ndinagwa pansi ndi kumva mawu akuti, ‘Saulo, Saulo, n’chifukwa chiyani ukundizunza?’+ 8 Ine ndinayankha kuti, ‘Ndinu ndani, Mbuyanga?’ Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndine Yesu Mnazareti, amene iwe ukumuzunza.’+ 9 Amuna amene anali nane+ anaonadi kuwalako, koma sanamve mawu a amene anali kulankhula ndi ine.+ 10 Pamenepo ndinati, ‘Ndichite chiyani,+ Ambuye?’ Ambuyewo anandiuza kuti, ‘Imirira, pita ukalowe mu Damasiko, ndipo kumeneko ukauzidwa zonse zimene zakonzedwa kuti uchite.’+ 11 Koma popeza sindinali kuona chilichonse chifukwa cha ulemerero wa kuwalako, amuna amene ndinali nawo limodzi aja, anandigwira dzanja mpaka kukafika ku Damasiko.+
12 “Tsopano Hananiya, munthu woopa Mulungu malinga ndi Chilamulo, amene anali ndi mbiri yabwino+ pakati pa Ayuda onse okhala kumeneko, 13 anabwera kwa ine. Ataima pafupi nane, anati, ‘M’bale wanga Saulo, yambanso kuona!’+ Nthawi yomweyo ndinakweza maso anga kumuyang’ana. 14 Ndiyeno iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu+ wakusankha+ kuti udziwe chifuniro chake, ndi kuti uone+ Wolungamayo+ ndi kumva mawu a pakamwa pake.+ 15 Pakuti udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zinthu zimene waona ndi kumva.+ 16 Nanga ukuchedweranji? Nyamuka, ubatizidwe+ ndi kusamba+ kuti uchotse machimo ako mwa kuitana pa dzina lake.’+
17 “Koma nditabwerera ku Yerusalemu,+ ndipo pamene ndinali kupemphera m’kachisi, ndinayamba kuona masomphenya.+ 18 M’masomphenyawo ndinaona Ambuye akundiuza kuti, ‘Fulumira, tuluka mu Yerusalemu msanga, chifukwa iwo sadzavomereza+ umboni wako wonena za ine.’ 19 Ndipo ine ndinanena kuti, ‘Ambuye, iwowo akudziwa bwino kwambiri kuti anthu amene anali kukukhulupirirani ndinali kuwaponya m’ndende+ ndi kuwakwapula m’sunagoge ndi sunagoge.+ 20 Komanso pamene magazi a Sitefano+ mboni yanu anali kukhetsedwa, ine ndinali kuonerera ndi kuvomereza zimenezo.+ Ndinenso amene ndinali kuyang’anira malaya akunja a anthu amene anali kumuphawo.’ 21 Koma anandiuzabe kuti, ‘Nyamuka, chifukwa ndidzakutumiza kutali kwa anthu a mitundu ina.’”+
22 Iwo anali kumumvetsera mpaka pa mawu amenewa. Kenako anafuula kuti: “Munthu ameneyu asapezekenso padziko lapansi, chifukwa sakuyenera kukhala ndi moyo!”+ 23 Koma popeza anali kufuula ndi kuponya malaya awo akunja komanso fumbi m’mwamba,+ 24 mkulu wa asilikali analamula kuti alowe naye kumpanda wa asilikali. Iye anati ayenera kumufunsa mafunso kwinaku akumukwapula, kuti adziwe bwino chimene chachititsa kuti anthu amukuwize+ choncho. 25 Koma atamugoneka kuti amukwapule, Paulo anafunsa kapitawo wa asilikali amene anali ataima pamenepo kuti: “Kodi anthu inu, malamulo amakulolani kukwapula munthu amene ndi Mroma,+ mlandu wake usanazengedwe?” 26 Kapitawo wa asilikali uja atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali ndi kukamuuza kuti: “N’chiyani chimene mukufuna kuchita? Munthu uyutu ndi Mroma.” 27 Pamenepo mkulu wa asilikaliyo anafika pafupi ndi kunena kuti: “Tandiuza, Kodi n’zoona ndiwe Mroma?”+ Iye anati: “Inde.” 28 Mkulu wa asilikaliyo anati: “Ine ndinagula ufulu umenewu wokhala nzika ndi ndalama zambiri.” Paulo anati: “Koma ine wanga ndinachita kubadwa+ nawo.”
29 Nthawi yomweyo amuna amene anafuna kumufufuza mwa kumuzunza aja anachoka n’kumusiya yekha. Nayenso mkulu wa asilikali uja anachita mantha atadziwa kuti ndi Mroma+ ndiponso kuti anamumanga.
30 Tsiku lotsatira, pofunitsitsa kudziwa chenicheni chimene Ayudawo anali kumuimbira mlandu, anamumasula. Atatero analamula ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda kuti asonkhane pamodzi. Ndiyeno anabweretsa Paulo ndi kumuimiritsa pakati pawo.+
23 Pamene anali kuyang’anitsitsa Khoti Lalikulu la Ayudalo, Paulo anati: “Amuna inu, abale anga, ndachita zinthu popanda chikumbumtima changa kunditsutsa ngakhale pang’ono pamaso pa Mulungu+ mpaka lero.” 2 Atamva zimenezi Hananiya mkulu wa ansembe, analamula anthu amene anaimirira pafupi naye kuti amubwanyule+ pakamwa. 3 Pamenepo Paulo anamuuza kuti: “Uona, Mulungu akukantha, khoma* lopaka laimu+ iwe. Wakhala pamenepo kuti undiweruze motsatira Chilamulo,+ kodi ukuphwanyanso wekha Chilamulocho+ polamula kuti andimenye?” 4 Anthu amene anaima pafupi naye anati: “Kodi ukulalatira mkulu wa ansembe wa Mulungu?” 5 Pamenepo Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Pakuti Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+
6 Tsopano Paulo ataona kuti ena mwa iwo anali Asaduki+ ndipo ena anali Afarisi, anafuula m’khotimo kuti: “Amuna inu, abale anga, ine ndine Mfarisi,+ mwana wa Afarisi. Pano ndikuweruzidwa+ chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka+ kwa akufa.” 7 Atanena zimenezi, panabuka mkangano+ pakati pa Afarisi ndi Asaduki, ndipo khamulo linagawanika. 8 Pakuti Asaduki+ amanena kuti akufa sadzauka,+ kulibe angelo, kapena cholengedwa chauzimu, koma Afarisi amavomereza poyera kuti zonsezi zilipo. 9 Choncho panabuka phokoso lalikulu,+ ndipo alembi ena a gulu la Afarisi anaimirira ndi kuyamba kutsutsa mwaukali kuti: “Sitikupeza cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu.+ Koma ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye,+ . . .” 10 Mkanganowo utakula kwambiri, mkulu wa asilikali anachita mantha kuti anthuwo amukhadzulakhadzula Paulo. Chotero analamula asilikali+ kuti apite komweko kuti akamuchotse pakati pawo ndi kumubweretsa kumpanda wa asilikali.+
11 Koma tsiku lomwelo usiku, Ambuye anaimirira pambali pake+ ndi kunena kuti: “Limba mtima!+ Pakuti wandichitira umboni mokwanira+ mu Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.”+
12 Kutacha, Ayuda anakonza chiwembu+ ndi kulumbira mwa kudzitemberera+ kuti sadya kapena kumwa kanthu kufikira atapha Paulo.+ 13 Analipo amuna oposa 40 amene anakonza chiwembu chochita kulumbirirachi. 14 Chotero anapita kwa ansembe aakulu+ ndi kwa akulu kukanena kuti: “Ife tachita lumbiro ndi kudzitemberera kuti sitilawa chakudya kufikira titapha Paulo. 15 Tsopano, inuyo pamodzi ndi Khoti Lalikulu la Ayuda, mufotokoze momveka bwino kwa mkulu wa asilikali. Mumuuze kuti amubweretse kwa inu, ngati kuti mukufuna kumvetsetsa bwino nkhani yokhudza munthu ameneyu.+ Koma asanafike n’komwe ife tidzakhala okonzeka kumupha.”+
16 Koma mwana wamwamuna wa mlongo wake wa Paulo anamva kuti anthuwo akonza zokamudikirira panjira,+ ndipo anapita ndi kukalowa kumpanda wa asilikali kukanena zimenezi kwa Paulo. 17 Choncho Paulo anaitana mmodzi mwa akapitawo a asilikali ndi kunena kuti: “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali, pakuti ali ndi mawu oti amuuze.” 18 Choncho mwamunayo anamutengadi ndi kupita naye kwa mkulu wa asilikali, ndipo anamuuza kuti: “Mkaidi uja Paulo, anandiitana ndi kundipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu, akuti ali ndi mawu oti akuuzeni.” 19 Mkulu wa asilikali uja anamugwira+ dzanja mnyamatayo ndi kupita naye pambali. Kumeneko anayamba kumufunsa kuti: “N’chiyani chimene ukufuna kundiuza?” 20 Iye anati: “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mupititse Paulo kubwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda mawa, ngati kuti iwo akufuna kumvetsa bwino za iye.+ 21 Koma chonde musalole kuti akunyengerereni, pakuti amuna oposa 40 akumudikirira panjira.+ Amenewa achita kulumbira modzitemberera kuti sadya kapena kumwa kanthu kufikira atamupha.+ Moti panopa akonzeka, akungoyembekezera chilolezo chanu.” 22 Pamenepo mkulu wa asilikaliyo anauza mnyamatayo kuti azipita atamulangiza kuti: “Usauze aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”
23 Ndiyeno anaitanitsa akapitawo awiri a asilikali ndi kuwauza kuti: “Uzani asilikali 200 kuti akonzekere kuyenda mpaka kukalowa mu Kaisareya cha m’ma 9 koloko* usiku uno. Pakhalenso amuna 70 okwera mahatchi* ndi asilikali 200 a mikondo. 24 Muwapatsenso nyama zonyamula katundu kuti akwezepo Paulo ndi kukamufikitsa kwa bwanamkubwa Felike ali wotetezeka.” 25 Ndiyeno iye analemba kalata yotere:
26 “Ine Kalaudiyo Lusiya, ndikulembera inu wolemekezeka, Bwanamkubwa Felike:+ Landirani moni! 27 Munthu uyu anagwidwa ndi Ayuda ndipo anali pafupi kumupha. Koma ine ndinafika mwadzidzidzi ndi gulu la asilikali n’kumulanditsa,+ chifukwa ndinamva kuti iyeyu ndi Mroma.+ 28 Choncho ine pofuna kudziwa chimene anapalamula, ndinapita naye kubwalo la Khoti lawo Lalikulu.+ 29 Kumeneko ndinapeza kuti akumuimba mlandu pa nkhani zokhudza Chilamulo chawo.+ Koma sanapezeke ndi mlandu uliwonse woyenera chilango cha imfa kapena kuponyedwa m’ndende.+ 30 Komabe popeza andiululira za chiwembu+ chimene amukonzera munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga, ndipo ndalamula omuimba mlanduwo kuti adzamuneneze mlanduwo pamaso panu.”+
31 Pamenepo asilikali+ amenewa anatenga Paulo usiku, monga anawalamulira ndi kupita naye ku Antipatiri. 32 M’mawa wake analola amuna okwera mahatchi aja kuti apitirire naye, ndipo iwo anabwerera kumpanda wa asilikali. 33 Amuna okwera mahatchiwo analowa mu Kaisareya+ ndi kupereka kalata ija kwa bwanamkubwa ndipo anaperekanso Paulo. 34 Choncho iye anaiwerenga ndi kufunsa chigawo chimene anali kuchokera, ndipo anapeza kuti+ ndi wochokera ku Kilikiya.+ 35 Pamenepo anati: “Ndimvetsera mlandu wako wonse, okuimba mlanduwo akafika.”+ Ndipo analamula kuti amusunge m’nyumba ya mfumu Herode ndi kumuyang’anira.
24 Patapita masiku asanu, kunafika mkulu wa ansembe Hananiya+ pamodzi ndi akulu ena, komanso munthu wina wodziwa kulankhula, dzina lake Teritulo. Iwo ananeneza+ Paulo kwa bwanamkubwa.+ 2 Teritulo atapatsidwa mwayi kuti alankhulepo, anayamba kuneneza Paulo. Iye anati:
“Tili pa mtendere wochuluka+ chifukwa cha inu, komanso zinthu zikusintha mu mtundu wathuwu chifukwa cha nzeru zanu zoona patali. 3 Choncho nthawi zonse komanso kulikonse, Inu Wolemekezeka+ a Felike, ife timayamikira kwambiri kulandira nzeru zanuzo. 4 Koma kuti ndisakutayitseni nthawi, ndikupempha chonde kuti mumve mawu athu pang’ono, mwa kukoma mtima kwanu. 5 Ife tapeza kuti munthu uyu ndi wovutitsa kwabasi,+ ndipo akuyambitsa zoukira boma+ pakati pa Ayuda onse padziko lapansi kumene kuli anthu. Ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lampatuko wa Anazareti.+ 6 Iyeyu anayesanso kudetsa kachisi,+ ndipo tinamugwira. 7* —— 8 Mutamufunsa, mungathe kutsimikizira nokha zonse zimene tikumunenezazi.”
9 Atanena zimenezi Ayuda nawonso analowerera kumuukira. Iwo anali kunena motsindika kuti zimenezo n’zoonadi. 10 Pamene bwanamkubwayo anagwedezera Paulo mutu kuti alankhule, Paulo anayankha kuti:
“Ine podziwa bwino kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu kwa zaka zambiri, ndine wokondwa kuti ndilankhule podziteteza+ pa zimene akundinenezazi. 11 Inu mukhoza kupeza umboni wakuti sipanapite masiku 12 kuchokera pamene ine ndinapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu.+ 12 Ndipo iwowa sanandipezepo m’kachisi+ ndikutsutsana ndi wina aliyense, ngakhale kuyambitsa chipolowe+ m’masunagoge kapena pena paliponse mumzindawu. 13 Ngakhalenso panopa sangathe kukupatsani umboni+ wa zimene akundinenezazi. 14 Komatu ndikuvomereza izi kwa inu: Njira yolambirira imene iwo akuitcha ‘gulu lampatuko,’ ndi njira imene ine ndikuchitira utumiki wopatulika kwa Mulungu wa makolo anga.+ Pakuti ndimakhulupirira zonse zimene zili m’Chilamulo+ ndi Zolemba za aneneri. 15 Ndipo ine ndili ndi chiyembekezo+ mwa Mulungu, chimenenso anthu awa ali nacho, kuti kudzakhala kuuka+ kwa olungama+ ndi osalungama omwe.+ 16 Pambali imeneyi, ndikuyesetsa mwakhama, kuchita mozindikira+ kuti ndisapalamule kwa Mulungu kapena kwa anthu. 17 Choncho pambuyo pa zaka zambiri, ndinabwera kudzapatsa mtundu wanga mphatso zachifundo, ndiponso kudzapereka nsembe.+ 18 Pamene ndinali kuchita zimenezi, anandipeza m’kachisi nditadziyeretsa monga mwa mwambo,+ koma panalibe khamu la anthu kapena wochita phokoso. Kumeneko kunali Ayuda ena ochokera m’chigawo cha Asia. 19 Amenewo ndiwo anali oyenera kupezeka pano pamaso panu kudzandineneza ine akanakhala ndi chifukwa chondiimbira mlandu.+ 20 Kapena, muwalole anthu ali panowa, afotokoze okha ngati anandipeza ndi cholakwa chilichonse pamene ndinaimirira pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. 21 Mawu amodzi okha amene ine ndinafuula, pamene ndinaimirira pakati pawo ndi akuti, ‘Ine lero ndikuweruzidwa pamaso panu chifukwa cha nkhani ya kuuka kwa akufa!’”+
22 Komabe Felike,+ ankadziwa bwino kwambiri nkhani yokhudza Njira imeneyi,+ choncho anaimitsa mlanduwo ndi kunena kuti: “Ndidzagamula mlandu wanuwu akadzafika Lusiya+ mkulu wa asilikali.” 23 Choncho analamula kapitawo wa asilikali kuti amuyang’anire munthuyu ndi kumupatsako ufulu, ndi kuti asaletse munthu aliyense mwa anthu a mtundu wake kumutumikira.+
24 Patapita masiku angapo, Felike+ anafika pamodzi ndi mkazi wake Durusila, amene anali mayi wachiyuda.+ Choncho Felike anaitanitsa Paulo ndi kumumvetsera pamene anali kufotokoza za kukhulupirira Khristu Yesu.+ 25 Koma pamene anali kulankhula za chilungamo,+ za kudziletsa,+ ndi za chiweruzo+ chimene chikudzacho, Felike anachita mantha ndipo anayankha kuti: “Basi, padakali pano ungapite, ndikadzapeza nthawi ndidzakuitananso.” 26 Pa nthawi imodzimodziyo, anali kuyembekezera kuti Paulo amupatse ndalama.+ Pa chifukwa chimenechi anali kumuitanitsa kawirikawiri n’kumakambirana naye.+ 27 Koma zaka ziwiri zitatha, Felike anachoka ndipo Porikiyo Fesito ndi amene analowa m’malo mwake. Koma popeza kuti Felike ankafuna kuti Ayuda azimukonda,+ anangomusiya m’ndende Paulo.
25 Patatha masiku atatu Fesito atayamba kulamulira+ m’chigawocho, anapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kaisareya.+ 2 Kumeneko ansembe aakulu ndi amuna olemekezeka pakati pa Ayuda anamuuza zambiri+ zoneneza Paulo. Ndiyeno anayamba kumuchonderera, 3 ndi kumupempha kuti awakomere mtima mwa kuitanitsa munthuyu kuti abwere ku Yerusalemu, kuti iwo amudikirire+ panjira ndi kumupha. 4 Koma Fesito anawayankha kuti Paulo akuyenera kusungidwa ku Kaisareya, ndi kuti posachedwa nayenso anyamuka kupita komweko. 5 Ndiyeno anati: “Amene ali ndi maudindo pakati panu, tipitire limodzi kuti ngati pali cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu akamuimbe mlandu.”+
6 Choncho iye atakhala nawo kumeneko kwa masiku osapitirira 8 kapena 10, anapita ku Kaisareya. Ndipo tsiku lotsatira anakhala pampando woweruzira milandu+ ndi kuitanitsa Paulo kuti abwere naye. 7 Paulo atafika, Ayuda amene anabwera kuchokera ku Yerusalemu, anaima momuzungulira n’kumamuneneza milandu yoopsa yambiri,+ imene sanathe kupereka umboni wake.
8 Koma Paulo podziteteza anati: “Ine sindinachimwire Chilamulo cha Ayuda, kapena kachisi,+ kapena Kaisara.”+ 9 Koma pofuna kuti Ayudawo amukonde,+ Fesito anayankha Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhani imeneyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?”+ 10 Paulo anayankha kuti: “Ine ndaimirira kutsogolo kwa mpando woweruzira milandu wa Kaisara,+ kumene ndiyenera kuweruzidwa. Ayuda+ sindinawalakwire chilichonse, monga mmene inunso mukuonera. 11 Ngati ndilidi wolakwa,+ ndipo ndachita chinthu choyenera imfa, sindikukana kufa.+ Koma ngati pa zimene awa akundinenezazi palibe chinthu chotero, palibe munthu amene angandipereke kwa iwo kuti awakondweretse. Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!”+ 12 Ndiyeno Fesito atalankhula ndi bungwe la aphungu, anayankha kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekera kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.”
13 Tsopano patapita masiku angapo, Mfumu Agiripa* ndi Berenike anafika ku Kaisareya pa ulendo wa boma wokapereka ulemu kwa Fesito. 14 Pamene anali kumeneko masiku angapo, Fesito anafotokozera mfumuyo nkhani yokhudza Paulo. Iye ananena kuti:
“Pali munthu wina amene Felike anamusiya m’ndende, 15 ndipo pamene ndinali ku Yerusalemu, ansembe aakulu komanso akulu a Ayuda anabwera kudzamuneneza.+ Anali kupempha kuti apatsidwe chiweruzo chakuti aphedwe. 16 Koma ine ndinawayankha kuti, Aroma sachita zinthu mwa njira imeneyo. Iwo sapereka munthu m’manja mwa omuneneza pongofuna kuwakondweretsa, munthu wonenezedwayo+ asanapatsidwe mwayi woonana pamasom’pamaso ndi omunenezawo kuti alankhule mawu odziteteza pa mlanduwo. 17 Choncho onse atafika kuno, sindinachedwe, koma tsiku lotsatira ndinakhala pampando woweruzira milandu ndi kuitanitsa munthuyo kuti abwere naye. 18 Omunenezawo ataimirira, sanatchule mlandu uliwonse+ wa zoipa zimene ndinali kuganiza zokhudza munthu ameneyu. 19 Iwo anali kungotsutsana naye nkhani zokhudzana ndi kulambira+ kwawo mulungu, ndi za munthu wina wake wotchedwa Yesu amene anafa koma Paulo akupitiriza kunena motsimikiza kuti ali moyo.+ 20 Choncho pothedwa nzeru ndi mkangano wa nkhani zimenezi, ndinamufunsa ngati akufuna kupita ku Yerusalemu kuti nkhanizi zikaweruzidwire kumeneko.+ 21 Koma pamene Paulo anapempha+ kuti timusunge kuti akamve chigamulo cha Wolemekezeka, ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”
22 Pamenepo Agiripa anauza Fesito kuti: “Inenso ndikufuna ndimve ndekha munthu ameneyu+ akulankhula.” Iye anati: “Mawa mudzamumvetsera.” 23 M’mawa wake, Agiripa ndi Berenike anabwera ndi ulemu waukulu wachifumu.+ Analowa m’chipinda chosonkhanira pamodzi ndi akuluakulu a asilikali komanso akuluakulu a mumzindawo, ndipo Fesito atalamula, anamubweretsa Paulo. 24 Ndiyeno Fesito ananena kuti: “Mfumu Agiripa ndi anthu nonse amene muli nafe pano, mukumuona munthu uyu. Ayuda onse anandipempha ine ku Yerusalemu komanso kuno, mofuula kuti iyeyu sayeneranso kukhala ndi moyo.+ 25 Koma ine ndinaona kuti sanachite chilichonse choyenera imfa.+ Choncho iyeyu atapempha kuti akaonekere kwa Wolemekezeka,+ ndinaganiza zomutumiza. 26 Koma ndilibe chenicheni chimene ndingalembere Mbuyanga chokhudza munthuyu. Choncho ndamubweretsa pamaso panu, makamaka pamaso pa inu, Mfumu Agiripa, kuti mukamufunsa za nkhaniyi,+ ndipeze cholemba. 27 Chifukwa kwa ine, ndikuona kuti si chanzeru kutumiza mkaidi koma osanena milandu imene akumuneneza.”
26 Ndiyeno Agiripa+ anauza Paulo kuti: “Waloledwa kulankhula mbali yako.” Pamenepo Paulo anatambasula dzanja lake+ ndi kuyamba kulankhula modziteteza kuti:+
2 “Inu Mfumu Agiripa, ndine wosangalala kuti lero ndidziteteza pamaso panu, pa zinthu zonse zimene Ayuda akundineneza.+ 3 Makamaka chifukwa chakuti ndinu katswiri pa miyambo yonse,+ komanso pa zimene Ayuda amakangana. Choncho ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.
4 “Ndithudi, moyo umene ndakhala+ kuyambira unyamata wanga, pakati pa anthu a mtundu wanga ndiponso mu Yerusalemu, ndi wodziwika bwino kwa Ayuda onse. 5 Ndi wodziwika bwino kwa Ayuda amene andidziwa ine kuchokera kale. Ndipo atafuna, angandichitire umboni kuti ndinalidi Mfarisi,+ wa m’gulu lampatuko lotsatira kulambira kwathu mokhwimitsa zinthu kwambiri.+ 6 Koma tsopano ndaimirira pano kuti ndiweruzidwe, chifukwa cha chiyembekezo+ pa lonjezo+ limene Mulungu anapereka kwa makolo athu. 7 Ndipo mafuko athu 12 akuyembekezera kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli, mwa kumuchitira utumiki wopatulika mosalekeza usana ndi usiku.+ Chotero Mfumu, Ayuda akundiimba mlandu chifukwa cha chiyembekezo chimenechi.+
8 “N’chifukwa chiyani anthu inu mukuona ngati n’zosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?+ 9 Inetu ndinali kuganiza mumtima mwanga kuti ndiyenera kuchita zambiri zotsutsana ndi dzina la Yesu Mnazareti. 10 Ndipo zimenezi ndinazichitadi mu Yerusalemu. Oyera ambiri ndinawatsekera m’ndende,+ nditapatsidwa mphamvu ndi ansembe aakulu.+ Pamene anafuna kuwapha, ine ndinali kuvomereza. 11 Nthawi zambiri ndinawapatsa chilango m’masunagoge onse,+ poyesa kuwakakamiza kuti akane chikhulupiriro chawo. Popeza ndinali nditakwiya nawo kwambiri, ndinafika pa kuwazunza ngakhale m’mizinda yakunja.
12 “Ndili kalikiliki ndi zimenezi, ndinanyamuka ulendo wopita ku Damasiko+ mwa mphamvu ndi chilolezo cha ansembe aakulu. 13 Koma ndili mumsewu dzuwa lili pamutu, Inu mfumu, ndinaona kuwala koposa kunyezimira kwa dzuwa kochokera kumwamba kutandizungulira pamodzi ndi amene ndinali nawo pa ulendowo.+ 14 Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu akundiuza m’Chiheberi kuti, ‘Saulo, Saulo, n’chifukwa chiyani ukundizunza ine? Ukungovutika popitiriza kuchita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake kuti imenye zisonga zotosera.’*+ 15 Koma ine ndinati, ‘Mbuyanga, ndinu ndani kodi?’ Ndipo Ambuye anati, ‘Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.+ 16 Komabe, dzuka ndi kuimirira.+ Pakuti ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndi mboni+ ya zinthu zonse, zimene waona ndi zimene ndidzakuonetsa zokhudza ine. 17 Ndidzakuonetsa zimenezi pamene ndidzakulanditsa kwa anthu awa ndi kwa anthu a mitundu ina, kumene ine ndikukutumiza.+ 18 Ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mu mdima+ ndi kuwatembenuzira ku kuwala.+ Kuwachotsa m’manja mwa Satana+ ndi kuwatembenuzira kwa Mulungu, kuti machimo awo akhululukidwe+ ndi kukalandira cholowa+ pamodzi ndi oyeretsedwa,+ mwa chikhulupiriro chawo mwa ine.’
19 “Chotero, Mfumu Agiripa, ine sindinachite zinthu zosonyeza kusamvera masomphenya a kumwambawo.+ 20 Koma kuyambira kwa okhala ku Damasiko+ ndi ku Yerusalemu,+ komanso m’dziko lonse la Yudeya ndi kwa anthu a mitundu ina,+ ndinafikitsa uthenga wakuti alape ndi kutembenukira kwa Mulungu mwa kuchita ntchito zosonyeza kulapa.+ 21 Chifukwa cha zimenezi, Ayuda anandigwira m’kachisi ndipo anafuna kundipha.+ 22 Komabe, popeza ndinalandira thandizo+ kuchokera kwa Mulungu, ndikupitiriza kuchitira umboni kwa anthu otchuka ndi kwa anthu wamba mpaka lero. Sindikunena kena kalikonse koma zokhazo zimene Zolemba za aneneri+ ndi za Mose+ zinaneneratu kuti zidzachitika. 23 Zolembazo zinaneneratu kuti Khristu adzavutika,+ ndipo monga woyamba kuukitsidwa kwa akufa,+ iye adzafalitsa kuwala+ mwa anthu awa ndi kwa anthu a mitundu ina.”+
24 Tsopano pamene anali kunena zinthu izi podziteteza, Fesito ananena mokweza mawu kuti: “Ukupenga+ iwe Paulo! Kuphunzira kwambiri kwakuchititsa misala!” 25 Koma Paulo anati: “Wolemekezeka a Fesito, inetu sindinachite misala ayi, koma ndikulankhula mawu a choonadi ndiponso anzeru. 26 Kunena zoona, inu mfumu amene ndikulankhula nanu mwaufulu chotere, mukudziwa bwino zimenezi. Ndili wotsimikiza kuti palibe ngakhale chimodzi mwa zinthu zimenezi, chimene simunachizindikire, pakuti izi sizinachitikire mseri.+ 27 Kodi inuyo, Mfumu Agiripa, mumakhulupirira Zolemba za aneneri? Ndikudziwa kuti mumazikhulupirira.”+ 28 Koma Agiripa anauza Paulo kuti: “M’kanthawi kochepa ungathe kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.” 29 Pamenepo Paulo anati: “Kaya m’kanthawi kochepa kapena m’nthawi yaitali, pemphero langa kwa Mulungu ndi lakuti, onse amene andimvetsera lero, osati inu nokha, akhale ngati ine, kupatulapo maunyolo okhawa.”
30 Pamenepo mfumu inaimirira. Chimodzimodzinso bwanamkubwa, Berenike ndi amuna amene anakhala nawo pamodzi. 31 Koma pochoka anayamba kukambirana kuti: “Munthu uyu sakuchita chilichonse choyenera imfa+ kapena kumangidwa.” 32 Ndipo Agiripa anauza Fesito kuti: “Akanakhala kuti sanapemphe kukaonekera kwa Kaisara, munthu ameneyu akanamasulidwa ndithu.”+
27 Tsopano ulendo wathu wa pamadzi wopita ku Italiya utatsimikizika,+ anapereka Paulo ndi akaidi ena m’manja mwa kapitawo wa asilikali dzina lake Yuliyo, wa m’gulu la asilikali la Augusito. 2 Ku Adiramutiyo tinakwera ngalawa imene inali pafupi kunyamuka ulendo wopita kumalo osiyanasiyana a m’mphepete mwa nyanja m’chigawo cha Asia. Kenako tinanyamuka, tilinso limodzi ndi Arisitako,+ yemwe anali Mmakedoniya wa ku Tesalonika. 3 Tsiku lotsatira tinafika ku Sidoni, ndipo Yuliyo anakomera mtima kwambiri+ Paulo ndipo anamulola kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalire.+
4 Titalowanso panyanja kuchokera kumeneko, tinayenda m’mphepete mwa chilumba cha Kupuro chimene chinatitchinjiriza ku mphepo imene inali kuwomba kuchokera kumene ife tinali kupita. 5 Tinayenda pakati pa nyanja molambalala Kilikiya ndi Pamfuliya, ndipo tinafika ku Mura, ku Lukiya. 6 Kumeneko kapitawo wa asilikali anapeza ngalawa yochokera ku Alekizandiriya+ imene inali kupita ku Italiya, ndipo anatikweza mmenemo. 7 Choncho tinayenda pang’onopang’ono kwa masiku ambiri ndipo tinafika ku Kinido movutikira. Polephera kupitirira chifukwa cha mphepo, tinadzera ku Salimone kuti chilumba cha Kerete chititchinge ku mphepo. 8 Titayenda movutikira m’mbali mwa chilumba chimenechi, tinafika pamalo ena otchedwa Madoko Okoma, amene anali pafupi ndi mzinda wa Laseya.
9 Popeza panali patapita kale nthawi yaitali, ndipo kuyenda panyanja tsopano kunali koopsa chifukwa ngakhale nthawi ya kusala kudya kwa tsiku la mwambo wophimba machimo+ inali itadutsa kale, Paulo anawapatsa malangizo. 10 Iye anawauza kuti: “Amuna inu, ndikuona kuti ulendowu tikauyamba panopa tiwonongetsa zambiri. Tiwonongetsa katundu ndi ngalawa, ngakhalenso miyoyo yathu.”+ 11 Koma kapitawo wa asilikaliyo anamvera woyendetsa ngalawa ndi mwiniwake wa ngalawayo m’malo momvera zimene Paulo ananena. 12 Popeza dokolo silinali labwino kukhalapo nyengo yachisanu, anthu ambiri analimbikitsa zakuti achoke pamalopo. Iwo ankafuna kuona ngati n’zotheka kukafika ku Finikesi kuti akakhale kumeneko nyengo yachisanu. Finikesi linali doko la Kerete loloza kumpoto chakum’mawa ndi kum’mwera chakum’mawa.
13 Ndiponso, mphepo ya kum’mwera itayamba kuwomba pang’onopang’ono, anaganiza kuti tsopano zimene anali kufuna zitheka. Choncho anakoka nangula n’kuyamba kuyenda m’mphepete mwa chilumba cha Kerete. 14 Koma posakhalitsa, mphepo yamkuntho+ yotchedwa Yulakilo inawomba ngalawayo. 15 Popeza ngalawa inali kuwombedwa ndi mphepo yamphamvu, ndipo sitinathe kuiwongolera kuti iyende moyang’anana ndi mphepoyo, tinagonja ndi kutengedwa nayo. 16 Tsopano tinayenda m’mphepete mwa chilumba china chaching’ono chotchedwa Kauda chimene chinali kutitchinjiriza ku mphepo. Komabe tinali kulephera kuwongolera bwato laling’ono limene ngalawayo inali kukoka.+ 17 Ndiyeno atakweza bwatolo m’ngalawa, anayamba kukulunga ngalawayo ndi zomangira kuti ilimbe. Ndipo poopa kuti ngalawa ingatitimire mumchenga pa Suriti,* iwo anatsitsa zingwe zomangira chinsalu cha ngalawa moti anali kukankhidwa ndi mphepo. 18 Koma popeza kuti mphepo yamkuntho inali kutiwomba ndi kutikankha mwamphamvu, tsiku lotsatira anthu anayamba kutaya katundu kuti ngalawa ipepukidwe.+ 19 Tsiku lachitatu, anataya ndi manja awo zingwe zokwezera chinsalu cha ngalawayo.
20 Tsopano poona kuti dzuwa kapena nyenyezi sizinaoneke kwa masiku ambiri, ndipo tinali kukankhidwa ndi chimphepo champhamvu,+ chiyembekezo choti tipulumuka chinatheratu. 21 Ndipo atakhala nthawi yaitali osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pawo+ ndi kunena kuti: “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga, osachoka ku Kerete kuja, ndithu zinthu sizikanawonongeka ndi kutayika chonchi.+ 22 Komabe, ndikukuuzani kuti mukhale osangalala, chifukwa palibe aliyense wa inu amene ataye moyo wake, koma ngalawa yokhayi iwonongeka. 23 Pakuti usiku mngelo+ wa Mulungu wanga, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika, anaima pafupi nane,+ 24 ndi kunena kuti, ‘Usaope Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara,+ ndipo taona! Chifukwa cha iwe, Mulungu mokoma mtima adzapulumutsa onse amene uli nawo pa ulendowu.’ 25 Choncho khalani osangalala amuna inu, pakuti ndikukhulupirira Mulungu+ kuti zonse zichitika ndendende mmene wandiuzira. 26 Komabe, ngalawa yathuyi iwonongeka pafupi ndi chilumba chinachake.”+
27 Tsopano usiku wa 14 unafika ndipo mphepo inali kutikankhira uku ndi uku panyanja ya Adiriya. Ndiyeno pakati pa usiku, ogwira ntchito mungalawa anayamba kuganiza kuti akuyandikira kumtunda. 28 Choncho anayeza kuzama kwa nyanja ndi kupeza kuti inali mamita 36. Atayenda kamtunda pang’ono anayezanso kuzama kwa nyanja ndi kupeza mamita 27. 29 Koma poopa kuti tikawomba miyala, anatsitsa anangula anayi kumbuyo kwa ngalawayo, ndipo anali kulakalaka kutangocha. 30 Tsopano ogwira ntchito m’ngalawamo anafuna kuthawamo. Anatsitsira bwato lija panyanja ponamizira kuti akufuna kutsitsa anangula kutsogolo kwa ngalawayo. 31 Koma Paulo anauza kapitawo wa asilikali ndi asilikaliwo kuti: “Anthu awa akapanda kukhalabe m’ngalawa muno, simupulumuka.”+ 32 Pamenepo asilikali anadula zingwe za bwatolo+ n’kulisiya kuti lipite.
33 Kutatsala pang’ono kucha, Paulo anayamba kulimbikitsa onse kuti adye chakudya. Iye anati: “Lero mwakwanitsa masiku 14 mukuchezera ndi kusala kudya, chifukwa mukungokhala osadya chilichonse. 34 Choncho ndikukulimbikitsani kuti mudye kuti zinthu zikuyendereni bwino. Pakuti ngakhale tsitsi+ limodzi la kumutu kwa aliyense wa inu siliwonongeka.” 35 Atanena zimenezi, anatenga mkate. Kenako anayamika+ kwa Mulungu pamaso pa onse n’kunyema mkatewo ndi kuyamba kudya. 36 Pamenepo onse anasangalala ndipo anayamba kudya chakudya. 37 Tonse pamodzi, m’ngalawamo tinalimo anthu 276. 38 Onse atadya ndi kukhuta, anayamba kutayira tirigu m’nyanja kuti ngalawa ija ipepukidwe.+
39 Potsirizira pake kutacha, sanathe kuzindikira dzikolo, koma anali kuona gombe linalake la mchenga, ndipo anafunitsitsa kuti ngati n’kotheka akaimitse+ ngalawa pamenepo. 40 Choncho anadula anangula ndi kuwagwetsera m’nyanja. Anamasulanso zingwe zomangira nkhafi zowongolera. Atakweza m’mwamba nsalu ya kutsogolo ya ngalawa, analunjika kugombelo. 41 Pamene anafika pachimulu cha mchenga m’madzimo, chimene mafunde anali kuchiwomba mbali zonse, ngalawa yawo inatitimira mumchengamo. Kutsogolo kwa ngalawayo kunakanirira pansi osasunthika, ndipo mafunde amphamvu anayamba kuwomba kumbuyo kwake moti inayamba kusweka zidutswazidutswa.+ 42 Zitatero asilikali anaganiza zopha akaidi, kuti pasapezeke aliyense wosambira n’kuthawa. 43 Koma kapitawo wa asilikali anafunitsitsa kuti Paulo akafike naye ali bwinobwino, choncho anawaletsa kuchita zimene amafunazo. Ndiyeno analamula odziwa kusambira kuti alumphire m’nyanjamo kuti akhale oyamba kukafika kumtunda. 44 Analamulanso ena onse kuti achite chimodzimodzi, ena pamatabwa ndipo ena pa zinthu zina zochokera kungalawayo. Ndipo pamapeto pake onse anafika kumtunda ali bwinobwino.+
28 Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita.+ 2 Ndipo anthu olankhula chinenero chachilendo kumeneko anatisonyeza kukoma mtima kwapadera.+ Iwo anasonkha moto ndi kutilandira bwino tonse chifukwa kunali kugwa mvula ndiponso kuzizira.+ 3 Koma pamene Paulo anatola kamtolo ka nkhuni ndi kukaika pamoto, panatuluka njoka ya mphiri chifukwa cha kutentha ndipo inaluma ndi kukanirira kudzanja la Paulo. 4 Anthu achinenero chachilendowo ataona njoka yapoizoni ikulendewera kudzanja lake, anayamba kuuzana kuti: “Ndithu munthu uyu ndi wopha anthu, chifukwa ngakhale wapulumuka panyanja, chilungamo sichinamulole kuti akhalebe ndi moyo.” 5 Koma iye anakutumulira njoka yapoizoniyo pamoto, ndipo sinamuvulaze.+ 6 Iwo anali kuyembekezera kuti atupa kapena agwa mwadzidzidzi n’kufa. Koma atayembekezera nthawi yaitali n’kuona kuti palibe choopsa chimene chikumuchitikira, anasintha maganizo awo ndi kuyamba kumunena kuti ndi mulungu.+
7 Tsopano pafupi ndi malo amenewa, panali minda ya munthu woyang’anira chilumbacho, dzina lake Papuliyo. Iyeyu anatilandira ndi kutichereza bwino kwambiri masiku atatu. 8 Koma kunapezeka kuti bambo ake a Papuliyo anali chigonere akuvutika ndi malungo* komanso kamwazi. Choncho Paulo analowa mmene bambowo anali ndi kupemphera, ndipo anasanjika manja ake+ pa iwo ndi kuwachiritsa.+ 9 Izi zitachitika, anthu ena onse pachilumbacho amene anali kudwala, nawonso anabwera kwa iye ndipo anawachiritsa.+ 10 Iwo anatilemekeza mwa kutipatsa mphatso zambiri, komanso pamene tinali kunyamuka ulendo wathu, anatipatsa zinthu zochuluka zimene tinali kuzisowa.
11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pangalawa ya ku Alekizandiriya.+ Ngalawa imeneyi inaima pachilumbapo kuyembekezera kuti nyengo yachisanu ithe, ndipo inali ndi chizindikiro cha “Ana Amapasa a Zeu.” 12 Kenako tinafika padoko ku Surakusa ndipo tinakhala pamenepo masiku atatu. 13 Pochoka kumeneko, tinazungulira ndi kukafika ku Regio. Patapita tsiku limodzi, kunayamba kuwomba mphepo ya kum’mwera, ndipo pa tsiku lachiwiri tinafika ku Potiyolo. 14 Kumeneko tinapeza abale ndipo anatichonderera kuti tikhale nawo masiku 7. Kenako tinapitiriza ulendo kulowera ku Roma. 15 Abale akumeneko atamva za ife, anabwera kudzatichingamira ku Msika wa Apiyo ndi ku Nyumba Zitatu za Alendo. Paulo atawaona, anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.+ 16 Pamapeto pake, titalowa mu Roma, Paulo analoledwa+ kumakhala yekha ndi msilikali womulondera.
17 Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana pamodzi, anawauza kuti: “Amuna inu, abale anga, ngakhale kuti sindinachite kanthu kotsutsana ndi anthu kapena mwambo wa makolo athu,+ ndinagwidwa mu Yerusalemu ndi kuperekedwa m’manja mwa Aroma monga mkaidi.+ 18 Ndipo iwowa atafufuza,+ anali ofunitsitsa kundimasula,+ pakuti sanapeze chifukwa mwa ine choyenera chilango cha imfa.+ 19 Koma Ayuda atapitiriza kutsutsa zimenezo, ndinakakamizika kupempha+ kudzaonekera kwa Kaisara, komatu sikuti ndinali ndi kanthu koti ndidzaneneze mtundu wanga ayi. 20 Pa chifukwa chimenechi, ndinapempha kuti ndikuoneni ndi kulankhula nanu, pakuti ndamangidwa ndi unyolo uwu+ chifukwa cha chiyembekezo+ cha Isiraeli.” 21 Iwo anamuyankha kuti: “Ife sitinalandire makalata alionse ochokera ku Yudeya onena za iwe. Palibenso aliyense mwa abale amene afika kuno, amene wanena kapena kukambapo choipa chilichonse chokhudza iwe. 22 Komabe tikufuna kumva maganizo ako, chifukwa kunena zoona, ife tonse timadziwa kuti gulu lampatuko limeneli+ amalinenera zoipa kwina kulikonse.”+
23 Pamenepo iwo anapangana naye tsiku, ndipo anabwera mwaunyinji kumene iye anali kukhala. Chotero kuyambira m’mawa mpaka madzulo, anawafotokozera nkhani yonse pochitira umboni mokwanira za ufumu wa Mulungu.+ Anachitira umboniwo mwa kugwiritsa ntchito mfundo zokopa zokhudza Yesu, kuchokera m’chilamulo cha Mose+ ndi mu Zolemba za aneneri.+ 24 Ena anayamba kukhulupirira+ zimene ananenazo, koma ena sanakhulupirire.+ 25 Choncho, popeza anali kutsutsana okhaokha, anayamba kuchoka, koma Paulo ananenabe mawu amodzi awa:
“Mzimu woyera unanena zoona kwa makolo anu kudzera mwa Yesaya mneneri. 26 Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma osazindikira ngakhale pang’ono. Kupenya mudzapenya ndithu, koma osaona ngakhale pang’ono.+ 27 Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Iwo atseka maso awo, kuti asaone ndi maso awo, asamve ndi makutu awo ndi kuti asazindikire ndi mtima wawo n’kutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+ 28 Chotero dziwani kuti njira ya Mulungu yopulumutsira anthu, yatumizidwa kwa anthu a mitundu ina.+ Ndipo mosakayikira, iwo adzaimvetsera.”+ 29* ——
30 Choncho Paulo anakhalabe m’nyumba yake yolipira kwa zaka ziwiri zathunthu,+ ndipo onse obwera kudzamuona anali kuwalandira ndi manja awiri. 31 Anali kuwalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu, mwaufulu wonse wa kulankhula+ popanda choletsa.
Ulendowu unali wa mtunda wa mamita 890, malinga ndi kufotokoza kwa mabuku achirabi, otengera mfundo za pa Yos 3:4.
Mawu ake enieni, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 5.
Mawu ake enieni, “ola la 9” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 4.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Mawu akuti “Njirayo” akutanthauza moyo ndi chiphunzitso chachikhristu.
Dzina lakuti “Dorika” n’chimodzimodzi ndi lakuti “Tabita.” Mayina onsewa amatanthauza “Mbawala.”
Mawu ake enieni, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Ena amati “patsindwi.”
Mawu ake enieni, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Ameneyu anali Herode Agiripa Woyamba.
Onani Zakumapeto 7.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Zikuoneka kuti anapita ku Yerusalemu.
“Mlaliki” palembali akutanthauza “mmishonale.”
Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
Mawu ake enieni, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko madzulo.
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Ameneyu anali Herode Agiripa Wachiwiri.
Zimenezi zinali ndodo zosongola zimene anali kutosera nyama zapagoli kuti ziyende mofulumira.
“Suriti” ndi malo awiri akuluakulu osazama a m’nyanja. Malo amenewa ali ku Libiya kumpoto kwa Afirika ndipo pamapezeka milu yambiri ya mchenga.
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.