Hoseya
1 Yehova analankhula+ ndi Hoseya+ mwana wa Beeri m’masiku+ a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya+ mafumu a Yuda, ndiponso m’masiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi+ mfumu ya Isiraeli. 2 M’masiku amenewo, Yehova anayamba kulankhula kudzera mwa Hoseya, ndipo Yehova anauza Hoseya kuti: “Pita+ ukakwatire mkazi amene adzachita dama. Pamenepo udzakhala ndi ana chifukwa cha dama la mkazi wakoyo. Pakuti mwanjira yofanana ndi zimenezi, dzikoli latembenuka ndi kusiya kutsatira Yehova chifukwa cha dama.”+
3 Pamenepo Hoseya anapita ndi kukakwatira Gomeri, mwana wamkazi wa Dibulaimu. Kenako Gomeri anatenga pakati ndipo anamuberekera mwana wamwamuna.+
4 Ndiyeno Yehova anauza Hoseya kuti: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Yezereeli,+ pakuti kwatsala kanthawi kochepa kuti ndiimbe Yezereeli* mlandu wokhetsa magazi, mlandu wa nyumba ya Yehu.+ Pamenepo ndidzathetsa ufumu wolamulira nyumba ya Isiraeli,+ 5 ndipo m’masiku amenewo ndidzathyola uta+ wa Isiraeli m’chigwa cha Yezereeli.”
6 Kenako Gomeri anatenganso pakati ndi kubereka mwana wamkazi. Ndiyeno Mulungu anauza Hoseya kuti: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Lo-ruhama,*+ pakuti sindidzachitiranso chifundo+ anthu a m’nyumba ya Isiraeli, chifukwa ndidzawathamangitsa.+ 7 Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda,+ ndipo Ine Yehova Mulungu wawo, ndidzawapulumutsa.+ Sindidzawapulumutsa ndi uta, lupanga, nkhondo, mahatchi* kapena ndi amuna okwera pamahatchi ayi.”+
8 Patapita nthawi, Gomeri anasiyitsa mwana wake Lo-ruhama kuyamwa, ndipo anatenganso pakati ndi kubereka mwana wamwamuna. 9 Pamenepo Mulungu anati: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Lo-ami,* chifukwa anthu inu sindinu anthu anga ndipo ine sindidzakhala Mulungu wanu.
10 “Ndiyeno ana a Isiraeli adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene munthu sangathe kuuyeza kapena kuuwerenga.+ Ndipo kumene anali kuuzidwa kuti, ‘Anthu inu sindinu anthu anga,’+ adzauzidwanso kuti, ‘Inu ndinu ana a Mulungu wamoyo.’+ 11 Pamenepo ana a Yuda ndi ana a Isiraeli adzasonkhanitsidwa pamodzi ndipo adzakhala ogwirizana.+ Iwo adzadziikira mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka m’dzikolo,+ chifukwa tsikuli lidzakhala lofunika kwambiri kwa Yezereeli.*+
2 “Uzani abale anu kuti, ‘Inu ndinu anthu anga,’+ ndipo alongo anu muwauze kuti, ‘Inu ndinu akazi osonyezedwa chifundo.’+ 2 Imbani mlandu mayi wanu.+ Muimbeni mlandu pakuti iye si mkazi wanga+ ndipo ine sindine mwamuna wake.+ Mayi wanuyo asiye dama lake ndi chigololo chake,*+ 3 kuti ndisamuvule ndi kumukhalitsa wamaliseche+ ngati tsiku limene anabadwa,+ kutinso ndisamuchititse kukhala ngati chipululu+ ndi dziko lopanda madzi+ ndiponso kuti ndisamuphe ndi ludzu.+ 4 Ana a mayiyo sindiwachitira chifundo,+ pakuti ndi ana obadwa chifukwa cha dama lake,+ 5 popeza mayi wawo wachita dama.+ Mayi amene anatenga pakati kuti awabereke wachita zinthu zochititsa manyazi+ ndipo wanena kuti, ‘Ndikufuna kutsatira amene anali kundikonda kwambiri+ ndiponso amene anali kundipatsa chakudya, madzi, zovala za ubweya wa nkhosa, nsalu, mafuta ndi zakumwa.’+
6 “Tsopano ine ndikutsekereza njira yake ndi mpanda waminga, ndipo ndidzamumangira mpanda wamiyala+ ndi kumutsekereza kuti asapeze njira zake.+ 7 Pamenepo iye adzathamangira amuna omukonda kwambiriwo, koma sadzawapeza.+ Adzawafunafuna koma sadzawapeza. Ndiyeno adzanena kuti, ‘Ndikufuna kubwerera kwa mwamuna wanga+ woyamba,+ pakuti zinthu zinali kundiyendera bwino nthawi imeneyo kusiyana ndi mmene zilili tsopano.’+ 8 Koma iye sanavomereze+ kuti ndine amene ndinali kumupatsa mbewu,+ vinyo wotsekemera* ndi mafuta. Sanavomerezenso kuti ndine amene ndinamuchulukitsira siliva ndi golide amene iye anali kumugwiritsa ntchito popembedza Baala.+
9 “‘Chotero ndidzatembenuka ndi kumulanda mbewu zanga pa nthawi yokolola. Ndidzalanda vinyo wanga wotsekemera pa nyengo yopanga vinyo.+ Ndidzamulandanso zovala zanga za ubweya wa nkhosa ndi nsalu zanga zimene amabisa nazo maliseche ake.+ 10 Tsopano ndidzamuvula kuti amuna omukonda kwambiriwo aone maliseche ake,+ ndipo palibe mwamuna amene adzamukwatula m’dzanja langa.+ 11 Pamenepo ndidzathetsa kusangalala kwake konse.+ Ndidzathetsa zikondwerero zake,+ chikondwerero cha tsiku lokhala mwezi,+ cha sabata ndi chikondwerero china chilichonse. 12 Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa+ ndi ya mkuyu+ imene iye anali kunena kuti: “Imeneyi ndi mphatso imene amuna ondikonda kwambiri anandipatsa.” Koma ine ndidzachititsa mitengoyo kukhala ngati nkhalango,+ ndipo zilombo zakutchire zidzaidya ndi kuiwononga. 13 Ndiyeno ndidzamuimba mlandu+ chifukwa cha masiku amene anapembedza zifaniziro za Baala+ zimene anali kuzifukizira nsembe zautsi.+ Nthawi imeneyi anali kuvala mphete* yake ndi zinthu zake zodzikongoletsera.+ Iye anali kutsatira amuna omukonda kwambiri+ ndipo ine anandiiwala,’+ watero Yehova.
14 “‘Choncho ndidzalankhula naye ndi kumukhutiritsa kuti achoke ndi kupita kuchipululu,+ ndipo ndidzalankhula naye momufika pamtima.+ 15 Kuyambira nthawi imeneyo mpaka m’tsogolo ndidzamupatsa minda yake ya mpesa.+ Ndidzamupatsanso chigwa cha Akori+ kuti chikhale ngati khomo lachiyembekezo. Pamenepo adzayankha ngati mmene anali kuyankhira ali mtsikana,+ ngatinso mmene anayankhira pa tsiku limene anatuluka m’dziko la Iguputo.’+ 16 Yehova wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo adzanditcha kuti Mwamuna wanga, ndipo sadzanditchanso kuti Mbuyanga.’*+
17 “‘Sindidzamulola kutchulanso mayina a zifaniziro za Baala,+ ndipo iye sadzakumbukiranso mayina awo.+ 18 Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi chilombo chakuthengo,+ cholengedwa chouluka m’mlengalenga ndi cholengedwa chokwawa panthaka, kuti ndithandize anthu anga. Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo padziko.+ Pamenepo ndidzawachititsa kukhala mwabata.+ 19 Ndidzalonjeza kukukwatira kuti ukhale wanga mpaka kalekale.*+ Ndidzalonjeza kukukwatira motsatira chilungamo, komanso chifukwa cha kukoma mtima kwanga kosatha ndi chifundo changa.+ 20 Ndidzalonjeza kukukwatira mokhulupirika ndipo udzadziwadi Yehova.’+
21 “Yehova wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo kumwamba ndidzakuyankha zopempha zake ndipo kumwambako kudzayankha zopempha za dziko lapansi.+ 22 Ndiyeno dziko lapansi lidzayankha mbewu,+ vinyo wotsekemera ndi mafuta, ndipo zimenezi zidzayankha Yezereeli.*+ 23 Pamenepo ndidzamufesa ngati mbewu zanga padziko lapansi.+ Ndidzachitira chifundo amene sanasonyezedwe chifundo+ ndipo ndidzauza anthu amene si anthu anga kuti: “Inu ndinu anthu anga,”+ ndipo iwo adzayankha kuti: “Inu ndinu Mulungu wathu.”’”+
3 Yehova anandiuza kuti: “Yambanso kukonda mkazi wokondedwa ndi mwamuna,+ mkazi amene akuchita chigololo. Ukamukonde ngati mmene Yehova akukondera ana a Isiraeli,+ ngakhale kuti iwo akutembenukira kwa milungu ina,+ imene amakonda kuipatsa nsembe za mphesa zouma zoumba pamodzi.”+
2 Chotero ndinagula mkaziyo ndi ndalama zasiliva 15+ ndi balere wokwana muyezo umodzi wa homeri* ndi hafu. 3 Kenako ndinamuuza kuti: “Ukhala ndi ine masiku ambiri.+ Usachite dama+ ndipo usagone ndi mwamuna wina.+ Inenso sindigona nawe.”
4 Ziyenera kukhala choncho chifukwa chakuti kwa masiku ambiri, ana a Isiraeli adzakhala opanda mfumu,+ kalonga, nsembe,+ chipilala chopatulika, efodi,+ ndi aterafi.*+ 5 Kenako ana a Isiraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo+ ndiponso Davide mfumu yawo.+ Iwo adzabwera kwa Yehova akunjenjemera+ ndipo adzafunafuna ubwino wake m’masiku otsiriza.+
4 Tamverani mawu a Yehova inu ana a Isiraeli. Yehova ali ndi mlandu ndi anthu okhala m’dzikoli,+ chifukwa m’dzikoli mulibe choonadi,+ kukoma mtima kosatha, ndiponso anthu a m’dzikoli amachita zinthu ngati kuti sadziwa Mulungu.+ 2 Kutembererana,+ kuchita zachinyengo,+ kuphana,+ kuba,+ ndi chigololo+ zafala m’dzikoli, ndipo kukhetsa magazi kukuchitika motsatizanatsatizana.+ 3 N’chifukwa chake dzikoli lidzalira maliro+ ndipo aliyense wokhala mmenemo adzalefukiratu pamodzi ndi zilombo zakutchire ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga. Nsomba zam’nyanja nazonso zidzafa.+
4 “Komabe, munthu asatsutse+ kapena kudzudzula anthu amenewa, chifukwa anthu a mtundu wako ali ngati munthu wotsutsana ndi wansembe.+ 5 Anthu inu mudzapunthwa masana+ ngati kuti ndi usiku. Ngakhalenso mneneri adzapunthwa pamodzi nanu,+ ndipo mayi wanu ndidzamuwononga.+ 6 Anthu anga adzawonongedwa chifukwa sakundidziwa.+ Popeza iwo akana kundidziwa,+ inenso ndidzawakana kuti azinditumikira ngati wansembe wanga.+ Popeza iwo aiwala lamulo la ine Mulungu wawo,+ inenso ndidzaiwala ana awo.+ 7 Pamene iwo achuluka, m’pamenenso akundichimwira kwambiri.+ M’malo mondipatsa ulemu, akundinyoza.+ 8 Iwo akupindula ndi machimo a anthu anga, ndipo amalakalaka tchimo la anthuwo.+
9 “Zimene zidzachitikira anthuwo zidzachitikiranso ansembe.+ Ndidzawaimba mlandu onsewa chifukwa cha njira zawo+ ndipo ndidzawabwezera zochita zawo.+ 10 Iwo adzadya koma sadzakhuta.+ Adzachita zachiwerewere ndi akazi koma sadzachulukana+ chifukwa chakuti asiya kumvera Yehova.+ 11 Dama, vinyo wakale ndi vinyo wotsekemera zimawononga nzeru za munthu.+ 12 Anthu anga amafunsira zinthu kwa mafano+ awo amtengo+ ndipo ndodo za m’manja mwawo zimawauza zochita. Amachita zimenezi chifukwa chakuti mtima wadama wawasocheretsa+ ndipo asiya kugonjera Mulungu wawo chifukwa cha damalo.+ 13 Iwo amapereka nsembe pamwamba pa mapiri+ ndipo amafukiza nsembe zautsi pazitunda.+ Amachitanso zimenezi pansi pa zimitengo zikuluzikulu, mitengo ya mlanje, ndi mitengo yaikulu, chifukwa ili ndi mthunzi wabwino.+ N’chifukwa chake ana anu aakazi amachita dama ndipo apongozi anu aakazi amachita chigololo.
14 “Sindidzalanga ana anu aakazi chifukwa chakuti akuchita dama, kapenanso apongozi anu aakazi chifukwa chakuti akuchita chigololo, pakuti amuna akumatengana ndi mahule+ ndipo akumaperekera nsembe limodzi ndi mahule aakazi a pakachisi.+ N’chifukwa chake anthu osamvetsa zinthuwa adzapondedwapondedwa.+ 15 Ngakhale kuti inu Aisiraeli mukuchita dama,+ Yuda asakhale wolakwa+ ndipo anthu inu musabwere ku Giligala.+ Musapitenso ku Beti-aveni+ kapena kulumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’+ 16 Isiraeli wakhala wamakani* ngati ng’ombe yamakani.+ Choncho kodi Yehova angawawete ngati nkhosa yamphongo yaing’ono pamalo otakasuka? 17 Efuraimu wagwirizana ndi mafano.+ Musiyeni aona!+ 18 Popeza mowa wawo watha,+ ayamba kuchita zachiwerewere ndi akazi.+ Oteteza+ anthu m’dzikolo akukonda zinthu zochititsa manyazi.+ 19 Mphepo yawakulunga m’mapiko ake,+ ndipo iwo adzachita manyazi ndi nsembe zawo.”+
5 “Imvani inu ansembe+ ndipo mvetserani inu a m’nyumba ya Isiraeli. Inunso a m’nyumba ya mfumu+ mvetserani, pakuti chiweruzochi chikukhudza inuyo, chifukwa mwakhala msampha+ ku Mizipa ndipo mwakhala ngati ukonde paphiri la Tabori.+ 2 Pakuti anthu amene andipandukira apha anthu ambiri,+ ngakhale kuti ine ndakhala ndikuwachenjeza onsewo.+ 3 Inetu ndimamudziwa bwino Efuraimu+ ndipo Isiraeli si wobisika kwa ine.+ Iwe Efuraimu ukuchita zachiwerewere ndi akazi+ ndipo Isiraeli wadziipitsa.+ 4 Zochita zawo zikuwalepheretsa kubwerera kwa Mulungu wawo+ chifukwa iwo ali ndi mtima wadama+ ndipo akana kudziwa Yehova.+ 5 Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+ ndipo Isiraeli ndi Efuraimu apunthwa ndi zochita zawo.+ Nayenso Yuda wapunthwa pamodzi nawo.+ 6 Iwo anapita kukafunafuna Yehova ali ndi nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, koma sanamupeze+ chifukwa anali atawachokera. 7 Achitira Yehova zinthu zachinyengo,+ chifukwa abereka ana achilendo.+ Tsopano pomatha mwezi, iwo adzakhala atadyedwa limodzi ndi zinthu zawo.+
8 “Lizani lipenga la nyanga ya nkhosa+ ku Gibeya!+ Lizani lipenga ku Rama! Fuulani mfuu ya nkhondo ku Beti-aveni!+ Tili pambuyo pako, iwe Benjamini!+ 9 Iwe Efuraimu, udzakhala chinthu chodabwitsa pa tsiku lako lolangidwa.+ Inetu ndauza mafuko a Isiraeli zinthu zoona zimene zidzawachitikira.+ 10 Akalonga a Yuda akhala ngati anthu osuntha malire.+ Ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ngati madzi. 11 Efuraimu waponderezedwa. Akusautsidwa moyenereradi,+ chifukwa anatsatira dala mdani wake.+ 12 Ine ndinali ngati njenjete*+ kwa Efuraimu, ndiponso ndinachititsa kuti nyumba ya Yuda iwole.
13 “Efuraimu anaona kudwala kwake ndipo Yuda anaona chilonda chake.+ Pamenepo Efuraimu anapita ku Asuri+ ndipo anatumiza amithenga kwa mfumu yaikulu.+ Koma mfumuyo sinathe kukuchiritsani anthu inu,+ ndipo sinathe kupoletsa chilonda chanu.+ 14 Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa Efuraimu+ ndiponso ngati mkango wamphongo kwa nyumba ya Yuda. Ineyo ndidzawakhadzulakhadzula ndekha ndi kuwataya ndipo sipadzakhala wowalanditsa.+ 15 Kenako ndidzabwerera kumalo anga kufikira iwo atalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo+ ndipo adzayamba kufunafuna nkhope yanga.+ Zinthu zikadzawavuta,+ adzandifuna.”+
6 “Bwerani anthu inu. Tiyeni tibwerere kwa Yehova,+ pakuti iye watikhadzulakhadzula+ koma adzatichiritsa.+ Wakhala akutivulaza koma adzamanga zilonda zathu.+ 2 Iye adzatikhalitsa ndi moyo pambuyo pa masiku awiri.+ Pa tsiku lachitatu adzatidzutsa ndipo tidzakhalanso ndi moyo pamaso pake. + 3 Ife tidzamudziwa Yehova ndipo tidzayesetsa kuti timudziwe bwino.+ N’zosakayikitsa kuti iye adzafika ndithu ngati mmene m’bandakucha+ umafikira.+ Adzabwera kwa ife ngati mvula yambiri.+ Adzabwera ngati mvula yomalizira imene imanyowetsa kwambiri nthaka ya padziko lapansi.”+
4 “Kodi ndikuchite chiyani iwe Efuraimu? Nanga iwe Yuda, ndikuchite chiyani?+ Anthu inu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kofanana ndi mitambo ya m’mawa, ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma. 5 N’chifukwa chake anthu amenewa ndidzawasema pogwiritsa ntchito aneneri.+ Ndidzawapha ndi mawu a m’kamwa mwanga.+ Chiweruzo chimene mudzalandire chidzakhala choonekera kwa anthu onse ngati kuwala.+ 6 Pakuti ndimakondwera ndi kukoma mtima kosatha,+ osati ndi nsembe.+ Ndimakondweranso ndi kudziwa Mulungu, osati ndi nsembe zopsereza zathunthu.+ 7 Koma iwo, mofanana ndi munthu wochokera kufumbi, aphwanya pangano.+ Andichitira zachinyengo kumalo kumene amakhala.+ 8 Giliyadi+ ndi tauni ya anthu ochita zinthu zopweteka anzawo, ndipo akhetsa magazi ambiri.+ 9 Gulu la ansembe lakhala gulu la achifwamba.+ Iwo amachita zinthu zofanana ndi za anthu obisalira munthu panjira.+ Amapha anthu m’mphepete mwa njira ku Sekemu+ chifukwa amangokhalira kuchita khalidwe lotayirira.+ 10 Ndaona zinthu zoopsa m’nyumba ya Isiraeli.+ Efuraimu akuchita dama mmenemo.+ Isiraeli wadziipitsa.+ 11 Koma inu anthu a ku Yuda, nthawi yoti musonkhanitsidwe ngati pa nthawi yokolola yakhazikitsidwa. Ine ndidzasonkhanitsanso anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.”+
7 “Nthawi zonse ndikafuna kuchiritsa Isiraeli,+ zolakwa za Efuraimu ndi zoipa za Samariya+ zimaonekera.+ Iwo amachita zachinyengo+ ndipo anthu akuba amalowa m’nyumba komanso gulu la achifwamba limasakaza zinthu panja.+ 2 Mumtima mwawo saganiza+ kuti ine ndidzakumbukira zochita zawo zonse zoipa.+ Tsopano ntchito zawo zawazungulira+ ndipo zili pamaso panga.+ 3 Iwo amasangalatsa mfumu ndi zoipa zawo, ndiponso amasangalatsa akalonga ndi chinyengo chawo.+ 4 Anthu onsewo ndi achigololo.+ Ali ngati ng’anjo yamoto imene wophika mkate waiyatsa. Ng’anjoyo yatentha kwambiri moti iye sakufunikira kuisonkhezera pamene akukanda ufa ndi kudikira kuti ufufume. 5 Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu, akalonga adzidwalitsa+ ndipo ali ndi ukali chifukwa cha vinyo.+ Mfumuyo yatambasula dzanja lake pamodzi ndi anthu onyoza. 6 Anthuwo atenthetsa mitima yawo ngati kuti aibweretsa pafupi ndi ng’anjo yamoto.+ Mitima yawoyo ikutentha mkati mwawo.+ Wophika mkate akugona usiku wonse. Pofika m’mawa, ng’anjoyo ikuyaka moto walawilawi.+ 7 Onsewo akutentha ngati ng’anjo yamoto, ndipo akuwononga oweruza awo. Mafumu awo onse agwa.+ Palibe aliyense wa iwo amene akundiitana.+
8 “Efuraimu amagwirizana ndi anthu a mitundu ina.+ Iye wakhala ngati mkate wozungulira umene wapsa mbali imodzi yokha.+ 9 Alendo alanda mphamvu zake,+ ndipo iye sakudziwa zimenezi.+ Mutu wake wonse wangoti mbuu ndi imvi, koma iye sakudziwa zimenezi. 10 Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+ koma iwo sanabwerere kwa Yehova Mulungu wawo.+ Sanamufunefune ngakhale kuti achita zinthu zonsezi.+ 11 Efuraimu ali ngati nkhunda yopusa,+ yopanda nzeru.+ Iwo apempha thandizo ku Iguputo+ ndiponso apita kudziko la Asuri.+
12 “Kulikonse kumene iwo angapite, ndidzawatchera ndi ukonde.+ Ndidzawagwira ngati zolengedwa zouluka m’mlengalenga.+ Ndidzawalanga mogwirizana ndi chenjezo limene ndinauza msonkhano wawo.+ 13 Tsoka kwa iwo+ chifukwa andithawa!+ Adzawonongedwa chifukwa chakuti aphwanya malamulo anga. Ine ndinali kufuna kuwawombola,+ koma iwo alankhula mabodza otsutsana nane.+ 14 Sanapemphe thandizo kwa ine ndi mtima wawo wonse+ ngakhale kuti anali kulira mofuula ali pamabedi awo. Anali kungokhala, osachita chilichonse, chifukwa anali ndi chakudya chambiri ndi vinyo wambiri wotsekemera.+ Nthawi zonse anali kuchita zinthu zonditembenukira.+ 15 Ine ndinawalangiza+ ndipo ndinalimbitsa manja awo.+ Koma iwo anali kukonza ziwembu, chotero anakhala otsutsana nane.+ 16 Anabwerera, koma sanapite ku chipembedzo choona.+ Anakhala ngati uta wosakungika.+ Akalonga awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha mwano wa lilime lawo lomwe.+ N’chifukwa chake iwo adzanyozedwa m’dziko la Iguputo.”+
8 “Ika lipenga la nyanga ya nkhosa pakamwa pako ndipo ulilize.+ Mdani akubwera ngati chiwombankhanga+ kudzaukira nyumba ya Yehova. Akubwera chifukwa Aisiraeli aphwanya pangano langa+ ndiponso aphwanya malamulo anga.+ 2 Iwo akundilirira kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife Aisiraeli tikukudziwani.’+
3 “Aisiraeli asiya kuchita zabwino,+ chotero mdani awathamangitse.+ 4 Iwo aika mafumu,+ koma osati mwa kufuna kwanga. Aika akalonga, popanda ine kuvomereza. Adzipangira mafano+ pogwiritsa ntchito siliva ndi golide wawo ndipo zimenezi zidzawawonongetsa.+ 5 Iwe Samariya, fano lako la mwana wa ng’ombe latayidwa.+ Mkwiyo wanga wayakira anthu ako.+ Kodi iwo adzalephera kudziyeretsa ku tchimo lawoli mpaka liti?+ 6 Zimenezi zachokera ku Isiraeli.+ Mmisiri ndiye anapanga fano la mwana wa ng’ombe la ku Samariya.+ Fanolo si Mulungu woona, chifukwa lidzangokhala ngati nkhuni zowazawaza.+
7 “Iwo akungofesa mphepo, ndipo adzakolola mphepo yamkuntho.+ Tirigu amene ali m’minda yawo sakukula.+ Mbewu zawo sizikuwapatsa ufa.+ Ngati zina mwa mbewuzo zingabereke, alendo adzazimeza.+
8 “Aisiraeli adzamezedwa+ moti adzakhala pakati pa mitundu ina ya anthu+ ngati chiwiya chosasangalatsa.+ 9 Iwo apita kudziko la Asuri+ ngati mbidzi yoyenda yokha.+ Koma Efuraimu walipira akazi kuti azigona nawo.+ 10 Ngakhale kuti akulipira akazi ochokera m’mitundu ina,+ ine ndidzasonkhanitsa anthu pamodzi. Kwa kanthawi, iwo adzamva ululu woopsa+ chifukwa cha katundu wolemetsa amene mafumu ndi akalonga asenzetsa anthu.
11 “Efuraimu wachulukitsa maguwa ansembe ndipo wachimwa.+ Iye wakhala ndi maguwa ansembe ndipo wawonjezera machimo ake.+ 12 Ine ndinamulembera zinthu zambiri zokhudza malamulo anga,+ koma anangoziona ngati zinthu zachilendo.+ 13 Iwo anali kupereka nsembe zanyama ngati mphatso kwa ine+ ndipo anali kuzidya, koma ine Yehova sindinakondwere nazo.+ Tsopano ndidzakumbukira zolakwa zawo. Ndidzawaimba mlandu chifukwa cha machimo awo+ ndiponso chifukwa chakuti iwo anabwerera ku Iguputo.+ 14 Isiraeli anaiwala amene anamupanga+ ndipo anayamba kumanga akachisi.+ Yuda nayenso anachulukitsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Koma ine ndidzatumiza moto m’mizinda yake ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za mumzinda uliwonse.”+
9 “Usasangalale iwe Isiraeli.+ Usachite zinthu mokondwera ngati mitundu ina ya anthu,+ pakuti wasiya Mulungu wako chifukwa cha dama.+ Ukukonda kulandira ndalama za uhule wako pamalo onse opunthira mbewu.+ 2 Malo opunthira mbewu ndiponso oponderamo mphesa sakukupatsa chakudya,+ ndipo vinyo wotsekemera akukukhumudwitsa.+ 3 Iwe sudzapitiriza kukhala m’dziko la Yehova.+ Efuraimu adzabwerera ku Iguputo+ ndipo adzadya zinthu zodetsedwa kudziko la Asuri.+ 4 Iye sadzapitiriza kupatsa Yehova nsembe zavinyo.+ Mulungu sadzakondwera ndi nsembe zake,+ chifukwa zili ngati chakudya cha pamaliro.+ Onse amene adzadya chakudyacho adzadziipitsa. Chakudya chawo chidzakhala chongokhutitsa iwowo basi, ndipo sichidzalowa m’nyumba ya Yehova.+ 5 Kodi anthu inu mudzachita chiyani pa tsiku la msonkhano ndi pa tsiku la chikondwerero cha Yehova?+ 6 Inutu mudzachoka chifukwa dzikolo lidzasakazidwa.+ Anthu a ku Iguputo adzakusonkhanitsani pamodzi+ ndipo anthu a ku Mofi+ adzakuikani m’manda. Zomera zoyabwa zidzamera pakatundu wanu wabwino wasiliva.+ M’mahema mwanu mudzamera zitsamba zaminga.+
7 “Masiku oti uyenderedwe adzafika,+ masiku oti ulipire adzakwana+ ndipo anthu a Isiraeli adzadziwa zimenezi.+ Mneneri adzapusa+ ndipo munthu wolankhula mawu ouziridwa adzalusa, chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako+ ndiponso chifukwa cha kuchuluka kwa chidani.”
8 Pa nthawi ina, mlonda+ wa Efuraimu anali ndi Mulungu wanga.+ Koma tsopano panjira zonse za mneneri,+ pali msampha wa wosaka mbalame.+ M’nyumba ya Mulungu wake muli chidani chachikulu. 9 Aisiraeli azama nazo zinthu zowononga+ ngati m’masiku a Gibeya.+ Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo+ ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.
10 “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zam’chipululu.+ Ndinaona makolo a anthu inu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu wongoyamba kumene kubereka.+ Iwo anapita kwa Baala wa ku Peori+ ndipo anadzipereka kwa chinthu chochititsa manyazicho.+ Anakhala onyansa ngati chinthu chimene anali kuchikondacho.+ 11 Ulemerero wa Efuraimu udzauluka ngati mmene imaulukira mbalame,+ moti sipadzakhalanso kubereka, kukhala ndi pakati, kapena kutenga pakati.+ 12 Pakuti ngakhale alere ana awo, ine ndidzawaphera anawo moti sadzakula n’kukhala amuna.+ Tsoka kwa iwo ndikadzawachokera!+ 13 Efuraimu ndamuona akuoneka ngati Turo atabzalidwa pamalo odyetserapo ziweto a msipu wobiriwira.+ Koma iye adzapititsa ana ake kokaphedwa.”+
14 Inu Yehova, apatseni zimene mukuyenera kuwapatsa.+ Chititsani kuti mimba zawo zizipita padera+ ndiponso mabere awo afote.
15 “Zoipa zawo zonse zinachitikira ku Giligala,+ ndipo ndinadana nawo kwambiri kumeneko.+ Chifukwa cha zochita zawo zoipa, ndidzawathamangitsa panyumba yanga.+ Sindidzapitiriza kuwakonda.+ Akalonga awo onse akuchita makani.+ 16 Efuraimu adzavulazidwa.+ Muzu wake udzauma,+ ndipo sadzaberekanso chipatso chilichonse.+ Komanso ngati angabereke, ndidzapha chipatso chokondedwa cha mimba yawo.”+
17 Mulungu wanga+ adzawakana chifukwa sanamumvere,+ ndipo iwo adzakhala othawa kwawo pakati pa mitundu ina.+
10 “Isiraeli ndi mtengo wa mpesa umene ukuwonongeka.+ Iye akupitiriza kubereka zipatso+ ndipo wachulukitsa maguwa ansembe mogwirizana ndi kuchuluka kwa zipatso zake.+ Pamene dzikolo likutukuka kwambiri m’pamenenso Aisiraeli akumanga zipilala zopatulika zokongola kwambiri.+ 2 Mtima wawo wakhala wachinyengo.+ Tsopano iwo adzapezeka ndi mlandu.
“Pali wina amene adzathyola maguwa awo ansembe ndipo adzasakaza zipilala zawo zopatulika.+ 3 Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Tilibe mfumu+ pakuti sitinaope Yehova. Ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi ikanatichitira chiyani?’
4 “Iwo amalankhula mawu opanda pake, amachita malumbiro abodza,+ amachita mapangano+ ndipo kusalungama kwafalikira ngati zomera zakupha m’mizere ya m’munda.+ 5 Anthu okhala ku Samariya adzachita mantha ndi fano la ku Beti-aveni+ la mwana wa ng’ombe. Pakuti anthuwo pamodzi ndi ansembe a mulungu wachilendo, amene anali kusangalala ndi fanolo chifukwa cha ulemerero wake, adzalilirira. Adzalirira fanolo chifukwa ulemerero wake udzachoka likadzatengedwa kupita kudziko lina.+ 6 Wina adzapititsa fanolo kudziko la Asuri ndi kukalipereka monga mphatso kwa mfumu yaikulu.+ Efuraimu adzachita manyazi+ ndipo Isiraeli adzachita manyazi ndi zoipa zimene anali kufuna kuchita.+ 7 Samariya pamodzi ndi mfumu yake adzakhalitsidwa chete,+ ngati kanthambi kothyoledwa mumtengo kamene kakuyandama pamadzi. 8 Malo okwezeka a ku Beti-aveni,+ omwe ndi tchimo la Isiraeli,+ adzawonongedwa. Minga ndi zitsamba zobaya*+ zidzamera pamaguwa awo ansembe.+ Anthu adzauza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’+
9 “Inu ana a Isiraeli, mwakhala mukuchimwa kuyambira m’masiku a Gibeya+ ndipo anthu anapitirizabe kuchita machimo kumeneko. Nkhondo ya ku Gibeya yomenyana ndi anthu osalungama sinawawononge onse.+ 10 Ndidzawalanga mtima wanga ukadzafuna.+ Anthu a mitundu ina adzasonkhana kuti alimbane nawo pa nthawi imene iwo adzamangidwe kugoli la zolakwa zawo ziwiri.+
11 “Efuraimu anali ng’ombe yaikazi yosaberekapo yophunzitsidwa bwino yokonda kupuntha mbewu,+ ndipo ine ndinapitirira khosi lake lokongola. Koma tsopano ndichititsa wina kukwera pamsana pa Efuraimu.+ Yuda akulima,+ Yakobo akumusalazira zibuma za dothi.+ 12 Bzalani mbewu za chilungamo+ ndipo kololani zipatso za kukoma mtima kosatha.+ Limani munda panthaka yabwino+ pamene muli ndi nthawi yofunafuna Yehova, kufikira iye atabwera+ ndi kukupatsani malangizo onena za chilungamo.+
13 “Anthu inu mwalima zoipa+ ndipo mwakolola kusalungama.+ Mwadya zipatso za zochita zanu zachinyengo,+ pakuti munali kudalira njira zanu+ ndi kuchuluka kwa anthu anu amphamvu.+ 14 Pakati pa anthu a mtundu wanu pachitika chisokonezo+ ndipo mizinda yanu yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzawonongedwa,+ ngati mmene Salimani anawonongera Beti-aribeli. Iye anachita zimenezi pa tsiku lankhondo, pamene amayi anaphwanyidwaphwanyidwa pamodzi ndi ana awo.+ 15 Inu anthu a ku Beteli, wina adzakuchitaninso zimenezi chifukwa ndinu anthu oipitsitsa.+ Ndithu, mfumu ya Isiraeli adzaikhalitsa chete m’bandakucha.”+
11 “Pa nthawi imene Isiraeli anali mnyamata ndinamukonda,+ ndipo ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.+
2 “Pamene iye anali kuitanidwa kwambiri,+ m’pamenenso anapitiriza kuchoka.+ Anayamba kupereka nsembe kwa zifaniziro za Baala+ ndipo anayamba kufukiza nsembe zautsi kwa zifaniziro zogoba.+ 3 Koma ine ndine amene ndinaphunzitsa Efuraimu kuyenda,+ amenenso ndinamunyamula m’manja mwanga+ koma iye sanavomereze kuti ndinamuchiritsa.+ 4 Ndinali kuwakoka mokoma mtima ndi mwachikondi,*+ moti kwa iwo ndinakhala ngati wochotsa goli m’khosi*+ mwawo ndipo mwachikondi ndinali kubweretsera aliyense wa iwo chakudya.+ 5 Iwo sadzabwerera kudziko la Iguputo, koma Asuri adzakhala mfumu yawo,+ chifukwa iwo anakana kubwerera kwa ine.+ 6 Lupanga lidzazungulira m’mizinda yake+ ndipo lidzawononga mipiringidzo yake ndi kupha+ anthu a m’mizindayo chifukwa cha zinthu zoipa zimene anali kufuna kuchita.+ 7 Anthu anga atsimikiza kuti akhale osakhulupirika kwa ine.+ Akuwaitana kuti abwerere kwa amene ali wokwezeka, koma palibe ngakhale ndi mmodzi yemwe amene akuimirira.
8 “Kodi ndikusiyirenji iwe Efuraimu?+ Kodi ndikuperekerenji kwa adani iwe Isiraeli?+ Kodi ndikusandutsirenji ngati Adima?+ Kodi ndikuchitirenji zofanana ndi zimene ndinachitira Zeboyimu?+ Mtima wanga wasintha+ ndipo pa nthawi imodzimodziyo wadzaza ndi chisoni. 9 Sindidzasonyeza mkwiyo wanga woyaka moto.+ Sindidzawononganso Efuraimu+ pakuti ndine Mulungu+ osati munthu. Ndine Woyera pakati panu+ ndipo sindidzabwera kwa inu nditakwiya. 10 Iwo adzayenda motsatira Yehova+ amene adzabangula ngati mkango.+ Inde adzabangula,+ ndipo ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.+ 11 Iwo adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Iguputo.+ Adzabweranso akunjenjemera ngati njiwa kuchokera kudziko la Asuri+ ndipo ndidzawachititsa kukhala m’nyumba zawo,” watero Yehova.+
12 “Efuraimu amalankhula mabodza okhaokha kwa ine.+ Kulikonse kumene ndingayang’ane ndikuona chinyengo cha Isiraeli, koma Yuda akuyendabe ndi Mulungu+ ndipo iye ndi wokhulupirika kwa Woyera Koposa.”
12 “Efuraimu akudya mphepo+ ndi kuthamangitsa mphepo ya kum’mawa tsiku lonse.+ Iye akuchulukitsa mabodza ndipo akuwononga zinthu zambiri.+ Wachita pangano ndi Asuri+ ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.
2 “Yehova ali ndi mlandu woti aimbe Yuda.+ Adzalanga Yakobo mogwirizana ndi njira zake+ ndipo adzamubwezera mogwirizana ndi zochita zake.+ 3 Pamene Yakobo anali m’mimba anagwira m’bale wake chidendene.+ Iye analimbana ndi Mulungu ndi mphamvu zake zonse.+ 4 Anapitiriza kulimbana ndi mngelo ndipo pamapeto pake anapambana.+ Analira pochonderera kuti amudalitse.”+
Mulungu anamupeza ku Beteli+ ndipo kumeneko Mulungu anayamba kulankhula nafe.+ 5 Iye ndi Yehova Mulungu wa makamu.+ Yehova ndilo dzina lake lomukumbukira nalo.+
6 “Koma iwe ubwerere kwa Mulungu wako.+ Usonyeze kukoma mtima kosatha+ ndi chilungamo+ ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.+ 7 M’manja mwa wamalonda muli sikelo yachinyengo+ ndipo iye amakonda kuba mwachinyengo.+ 8 Efuraimu akupitiriza kunena kuti, ‘Inetu ndalemeradi,+ ndapeza zinthu zamtengo wapatali.+ Palibe amene angapeze cholakwa chachikulu pa ntchito zanga zonse.’+
9 “Ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+ Koma ndidzakuchititsa kukhala m’mahema ngati pa masiku achikondwerero. 10 Ndinalankhula ndi aneneri+ ndipo ndinawaonetsa masomphenya ochuluka. Kudzera mwa aneneri, ndinali kupereka mafanizo ambiri.+
11 “Ku Giliyadi anthu akuchita zamatsenga+ ndiponso akulankhula zabodza.+ Ku Giligala akupereka nsembe ng’ombe zamphongo.+ Komanso maguwa awo ansembe ali ngati milu ya miyala m’mizere ya m’munda.+ 12 Yakobo anathawira kumunda wa ku Siriya+ ndipo Isiraeli+ anapitirizabe kugwira ntchito+ ndi kulondera nkhosa kuti apeze mkazi.+ 13 Yehova anatulutsa Isiraeli ku Iguputo pogwiritsa ntchito mneneri,+ ndipo mneneri analondera Isiraeli.+ 14 Efuraimu anakhumudwitsa kwambiri Mulungu.+ Magazi amene iye anakhetsa ali pa iyeyo+ ndipo Ambuye Wamkulu adzamubwezera chitonzo chake.”+
13 “Efuraimu akalankhula, anthu anali kunjenjemera. Iye anali wolemekezeka mu Isiraeli,+ koma anapezeka ndi mlandu wolambira Baala+ ndipo anafa.+ 2 Tsopano anthu ake akuchita machimo ena ndipo akugwiritsa ntchito siliva wawo popanga zifanizo zachitsulo chosungunula.+ Zifanizo zimenezo ndi mafano opangidwa mogwirizana ndi maganizo awo,+ koma zonsezi ndi ntchito za amisiri.+ Iwo amauza mafanowo kuti, ‘Amuna opereka nsembe apsompsone mafano a ana ang’ombe.’+ 3 Chotero iwo adzakhala ngati mitambo ya m’mawa+ ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma. Adzakhalanso ngati mankhusu* amene amauluzika kuchokera pamalo opunthira mbewu+ ndiponso ngati utsi umene umatuluka m’chumuni kudenga.*
4 “Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+ Panalibe Mulungu wina amene unali kumudziwa kupatulapo ine. Panalibenso mpulumutsi wina kupatulapo ine.+ 5 Ine ndinakudziwa uli m’chipululu,+ m’dziko la matenda otenthetsa thupi.+ 6 Iwe unakhuta chifukwa chakuti unali ndi zakudya zambiri.+ Unakhuta ndipo mtima wako unayamba kudzitukumula.+ N’chifukwa chake unandiiwala.+ 7 Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa iwo.+ Ndidzapitiriza kuwayang’ana ngati kambuku* amene wabisala m’mphepete mwa njira.+ 8 Ndidzawaukira ngati chimbalangondo chimene ana ake asowa+ ndipo ndidzang’amba zifuwa zawo, mmene muli mitima yawo. Ndidzawadya kumeneko ngati mkango.+ Chilombo chakuthengo chidzawakhadzulakhadzula.+ 9 Chifukwa chakuti zimene iwe Isiraeli unachita zinali zotsutsana ndi ine mthandizi wako,+ zimenezo zidzakuwononga.+
10 “Tsopano mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse m’mizinda yako yonse.+ Oweruza ako ali kuti amene unawauza kuti, ‘Ndipatseni mfumu ndi akalonga’?+ 11 Ndiyeno ndinakupatsa mfumu nditakwiya+ ndipo ndidzaichotsa nditakwiya.+
12 “Zolakwa za Efuraimu zakulungidwa pamodzi, ndipo machimo ake asungidwa.+ 13 Zowawa ngati za mkazi amene akubereka zidzamugwera.+ Iye ndi mwana wopanda nzeru+ chifukwa nthawi yoti abadwe ikakwana, sadzadziika pamalo amene ana amatulukira pochokera m’chiberekero.+
14 “Ine ndidzawawombola ku Manda*+ ndiponso ku imfa.+ Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+ Iwe Manda amene umawononga, kodi uli kuti?+ Koma Efuraimu sindimumverabe chisoni.+
15 “Ndipo iye akayamba kubereka ndi kutulutsa ana ngati bango,+ mphepo ya kum’mawa, mphepo ya Yehova idzabwera.+ Mphepo yake ikuchokera kuchipululu ndipo idzaumitsa chitsime chake ndi kuphwetsa kasupe wake.+ Ameneyo adzawononga chuma chimene chikuphatikizapo zinthu zosiririka.+
16 “Samariya adzaimbidwa mlandu+ chifukwa iye akupandukira Mulungu wake.+ Iwo adzagwetsedwa ndi lupanga.+ Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa+ ndipo akazi awo amene ali ndi pakati adzatumbulidwa.”+
14 “Iwe Isiraeli, bwerera kwa Yehova Mulungu wako+ pakuti wapunthwa mu zolakwa zako.+ 2 Bwerera kwa Yehova ndi mawu osonyeza kulapa.+ Anthu nonsenu uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu.+ Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife, ndipo mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe kwa inu.+ 3 Dziko la Asuri silidzatipulumutsa.+ Ife sitidzakwera pamahatchi.+ Sitidzauzanso ntchito ya manja athu kuti: “Inu Mulungu wathu!” chifukwa inu mumachitira chifundo mwana wamasiye.’*+
4 “Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo.+ Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga,+ chifukwa mkwiyo wanga wawachokera.+ 5 Ine ndidzakhala ngati mame kwa Isiraeli,+ ndipo iye adzaphuka ngati maluwa okongola. Mizu yake idzazama ngati mtengo wa ku Lebanoni. 6 Nthambi zake zidzaphukira ndipo adzakhala ndi ulemerero ngati mtengo wa maolivi.+ Fungo lake lonunkhira lidzakhala ngati mtengo wa ku Lebanoni. 7 Iwo adzakhalanso mumthunzi wake.+ Adzabzala mbewu ndipo adzaphuka ngati mpesa.+ Dzina lawo lidzakumbukiridwa ngati vinyo wa ku Lebanoni.
8 “Efuraimu adzanena kuti, ‘Kodi mafano ndi a chiyaninso kwa ine?’+
“Ine ndidzamva ndipo ndidzapitirizabe kumuyang’anira.+ Ine ndili ngati mtengo waukulu wa mkungudza wamasamba obiriwira+ ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.”
9 Ndani ali ndi nzeru kuti amvetse zinthu zimenezi?+ Wochenjera ndani kuti adziwe zimenezi?+ Pakuti njira za Yehova ndi zowongoka+ ndipo anthu olungama ndi amene adzayendamo,+ koma olakwa adzapunthwa m’njira zimenezo.+
Umenewu unali mzinda wachifumu kumene mafumu a Isiraeli anali kukhala, ngakhale kuti likulu lawo linali mzinda wa Samariya. Onani 1Mf 21:1.
Dzinali limatanthauza kuti, “Sanamuchitire Chifundo.”
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Dzinali limatanthauza kuti, “Iwo Si Anthu Anga.”
Dzinali limatanthauza kuti, “Mulungu Adzafesa Mbewu.”
Mawu ake enieni, “achotse dama lake pamaso pake ndi zochita zake zachigololo pakati pa mawere ake.”
Ena amati “wonzuna.”
Kapena kuti “chipini.” Onani Miy 11:22, mawu a m’munsi.
Kapena kuti “Baala wanga,” kutanthauza “Mwiniwake wa ine.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Ho 1:11.
“Homeri” imodzi ndi yofanana ndi malita 220.
“Aterafi” ndi milungu kapena mafano amene mabanja anali kupembedza.
Ena amati “wanthota.”
Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
Ena amati “kulasa.”
Mawu ake enieni, “Ndinali kuwakoka ndi zingwe za munthu ndiponso ndi zingwe zachikondi.” Mwina akufanizira ndi zimene kholo limachita likamaphunzitsa mwana kuyenda pogwiritsa ntchito zingwe.
Mawu ake enieni, “munsagwada.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Kapena kuti “tsindwi.”
Ena amati “nyalugwe.”
Onani Zakumapeto 5.
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”