Danieli
1 M’chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu+ mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu ndipo anazungulira mzindawo.+ 2 Kenako Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda m’manja mwake.+ Anaperekanso kwa iye zina mwa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona moti Nebukadinezara anazitengera kudziko la Sinara,+ kunyumba ya mulungu wake. Ziwiya zimenezi anakaziika m’nyumba ya mulungu wake yosungiramo chuma.+
3 Ndiyeno mfumu inauza Asipenazi, mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu+ kuti abweretse ena mwa ana a Isiraeli, ana a m’banja lachifumu, ndi ana a anthu olemekezeka,+ 4 amene analibe chilema chilichonse,+ ooneka bwino, ozindikira zinthu, anzeru,+ odziwa zinthu, omvetsa zinthu mwamsanga,+ amenenso akanatha kutumikira m’nyumba ya mfumu.+ Anawabweretsa kuti awaphunzitse kulemba* ndiponso chinenero cha Akasidi. 5 Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamulanso kuti tsiku lililonse iwo aziwapatsa zakudya zabwino+ za mfumu ndi vinyo wa mfumu. Inalamulanso kuti awasamalire kwa zaka zitatu ndipo zaka zimenezi zikadzatha, akayambe kutumikira mfumu.
6 Pakati pa anawo panali ana ena a ku Yuda. Mayina awo anali Danieli,+ Hananiya, Misayeli ndi Azariya,+ 7 koma mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu anapatsa anawa mayina ena.+ Danieli anamupatsa dzina lakuti Belitesazara,+ Hananiya anamupatsa dzina lakuti Sadirake, Misayeli anamupatsa dzina lakuti Mesake, ndipo Azariya anamupatsa dzina lakuti Abedinego.+
8 Koma Danieli anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa+ ndi zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wake. Choncho iye anapitirizabe kupempha mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu kuti amulole kuti asadzidetse ndi zakudyazo.+ 9 Chotero Mulungu woona anachititsa kuti mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu asonyeze Danieli kukoma mtima kosatha ndi chifundo.+ 10 Komabe mkulu wa nduna za panyumba ya mfumuyo anauza Danieli kuti: “Ine ndikuopa mbuye wanga mfumu, amene walamula kuti mupatsidwe zakudya ndi zakumwa zake.+ Ndiye n’chifukwa chiyani mukufuna kuti aone nkhope zanu zili zachisoni poyerekeza ndi ana ena amsinkhu wanu? Komanso, bwanji mukufuna kuikitsa mutu wanga pangozi kwa mfumu?” 11 Pamenepo Danieli anakalankhula ndi munthu amene anali kuwayang’anira, amene mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu+ uja anamuika kuti aziyang’anira Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya, ndipo anati: 12 “Chonde, yesani atumiki anufe kwa masiku 10. Lolani kuti azitipatsa zakudya zamasamba+ ndi madzi oti tizimwa. 13 Pambuyo pake mudzayerekeze mmene ifeyo tikuonekera ndi mmene ana amene akudya zakudya zabwino za mfumu akuonekera, ndipo mudzachitire atumiki anufe mogwirizana ndi zimene mudzaone.”
14 Pamapeto pake, munthu amene anali kuwayang’anira uja anawamvera pa nkhani imeneyi ndipo anawayesa kwa masiku 10. 15 Masiku 10 amenewo atatha, iwo anali kuoneka bwino kwambiri ndiponso matupi awo ankaoneka athanzi kuposa ana onse amene anali kudya zakudya zabwino za mfumu.+ 16 Choncho, wowayang’anira uja anapitirizabe kuwapatsa zakudya zamasamba+ m’malo mwa zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wake. 17 Tsopano Mulungu anawachititsa ana anayi amenewa kudziwa ndi kuzindikira zinthu zonse zolembedwa ndiponso anawapatsa nzeru.+ Danieli anali womvetsa bwino masomphenya ndi maloto amtundu uliwonse.+
18 Ndiyeno masiku amene mfumu inanena kuti adzabweretse ana aja pamaso pake anakwana.+ Zitatero mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu uja anabweretsa anawo pamaso pa Nebukadinezara. 19 Pamenepo mfumu inayamba kulankhula nawo ndipo pa ana onsewo, palibe aliyense amene anali ngati Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya.+ Chotero ana amenewa anapitiriza kutumikira mfumu.+ 20 Pa nkhani iliyonse imene mfumu inali kufunsira nzeru kwa iwo kuti imvetse bwino,+ inaona kuti iwo anali anzeru kuwirikiza maulendo 10 kuposa ansembe onse ochita zamatsenga+ ndi anthu onse olankhula ndi mizimu+ amene anali mu ufumu wake. 21 Chotero Danieli anapitiriza kukhala kumeneko mpaka chaka choyamba cha ulamuliro wa mfumu Koresi.+
2 M’chaka chachiwiri cha ufumu wa Nebukadinezara, Nebukadinezarayo analota maloto.+ Malotowo anamuvutitsa maganizo+ ndipo tulo tinamuthera. 2 Pamenepo mfumuyo inalamula kuti aitane ansembe onse ochita zamatsenga,+ anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi anthu ena ochita zamatsenga kuti adzauze mfumu maloto akewo.+ Anthu amenewa anafika ndi kuima pamaso pa mfumu. 3 Ndiyeno mfumuyo inawauza kuti: “Pali zimene ndalota, ndipo ndikuvutika maganizo kwambiri kuti ndidziwe malotowo.” 4 Pamenepo Akasidi anayankha mfumu m’chinenero cha Chiaramu+ kuti: “Inu mfumu mukhale ndi moyo mpaka kalekale.*+ Tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo tikumasulirani malotowo.”+
5 Mfumuyo inayankha Akasidiwo kuti: “Ine ndikulamula kuti: Amuna inu mukapanda kundiuza malotowo ndi kuwamasulira, mudzadulidwa nthulinthuli+ ndipo nyumba zanu zidzasanduka zimbudzi za anthu onse.+ 6 Koma mukandiuza malotowo ndi kuwamasulira, ine ndikupatsani mphatso, mphoto ndi ulemerero wochuluka.+ Choncho ndiuzeni malotowo ndipo muwamasulire.”
7 Pamenepo iwo anayankhanso kachiwiri kuti: “Inu mfumu, tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo ife tikumasulirani malotowo.”
8 Ndiyeno mfumuyo inanena kuti: “Ine ndikudziwa kuti amuna inu mukuzengereza dala chifukwa mwadziwa kuti ine ndalamula zimenezi. 9 Pakuti mukapanda kundiuza malotowo, chilango chija+ sichidzakuphonyani. Koma mwagwirizana kuti mundiuze mawu abodza+ kufikira zinthu zitasintha. Choncho ndiuzeni zimene ndalota. Mukatero, ndidziwa kuti mungathe kumasulira malotowo.”
10 Akasidiwo anayankha mfumuyo kuti: “Palibe munthu padziko lapansi amene angathe kuuza inu mfumu zimene mukufuna, pakuti palibe mfumu yaikulu kapena bwanamkubwa amene anauzapo wansembe wochita zamatsenga kapena munthu wolankhula ndi mizimu kapena Mkasidi kuti achite zimenezi. 11 Zimene inu mfumu mukufuna kuti tichite ndi zovuta, ndipo palibe munthu amene angakuuzeni maloto anu, kupatulapo milungu.+ Komano milunguyo siikhalanso pakati pa anthu.”+
12 Mfumu itamva zimenezi inapsa mtima ndipo inakwiya kwambiri,+ moti inanena kuti amuna onse anzeru a m’Babulo ayenera kuphedwa.+ 13 Lamulo limenelo linaperekedwa, ndipo amuna anzeru anatsala pang’ono kuphedwa, moti anthu anayamba kufunafuna Danieli ndi anzake kuti awaphe.
14 Pa nthawi imeneyo Danieli analankhula mwanzeru ndi mozindikira+ kwa Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali atanyamuka kale kuti akaphe amuna anzeru a m’Babulo. 15 Iye anafunsa Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu uja kuti: “Chavuta n’chiyani kuti mfumu ipereke lamulo lokhwima chonchi?” Pamenepo, Arioki anafotokoza nkhani yonse ija kwa Danieli.+ 16 Chotero Danieli anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.+
17 Kenako Danieli anabwerera kunyumba kwake ndipo anauza anzake aja, Hananiya, Misayeli ndi Azariya za nkhani imeneyi. 18 Anawauza zimenezi ndi cholinga choti iwo apemphe Mulungu wakumwamba+ kuti awachitire chifundo+ ndi kuwaululira chinsinsi chimenechi,+ kuti Danieli, anzakewo ndi amuna anzeru ena onse a m’Babulo asaphedwe.+
19 Ndiyeno usiku, chinsinsicho chinaululidwa kwa Danieli m’masomphenya.+ Pamenepo Danieli anatamanda+ Mulungu wakumwamba. 20 Iye anati: “Dzina la Mulungu likhale lotamandika+ kuyambira kalekale mpaka kalekale, pakuti nzeru ndi mphamvu ndi zake.+ 21 Iye amasintha nthawi ndi nyengo,+ amachotsa mafumu ndi kuika mafumu,+ amapereka nzeru kwa anthu anzeru ndiponso amachititsa kuti anthu ozindikira adziwe zinthu.+ 22 Amaulula zinthu zozama ndi zinthu zobisika+ ndipo amadziwa zimene zili mu mdima.+ Komanso wazunguliridwa ndi kuwala.+ 23 Ndikukutamandani ndi kukuyamikani,+ inu Mulungu wa makolo anga, chifukwa mwandipatsa nzeru+ ndi mphamvu. Tsopano mwandiuza zimene tinakupemphani, pakuti mwatidziwitsa zimene mfumu inali kufuna.”+
24 Zitatero, Danieli anapita kwa Arioki,+ amene mfumu inali itamutuma kuti akaphe amuna anzeru a m’Babulo.+ Anapita kwa iye n’kumuuza kuti: “Musaphe mwamuna aliyense wanzeru m’Babulo. Ndipititseni kwa mfumu,+ kuti ndikamasulire maloto ake.”
25 Mofulumira, Arioki anapititsa Danieli kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “Ndapeza mwamuna wamphamvu pakati pa anthu amene anatengedwa ukapolo+ ku Yuda yemwe angamasulire maloto anu mfumu.” 26 Mfumuyo inafunsa Danieli, amene anali kutchedwa kuti Belitesazara,+ kuti: “Kodi ungathe kundiuza maloto amene ndinalota ndi kuwamasulira?”+ 27 Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Chinsinsi chimene inu mfumu mukufuna kudziwa, amuna anzeru, anthu olankhula ndi mizimu, ansembe ochita zamatsenga ndi anthu okhulupirira nyenyezi, alephera kukuuzani.+ 28 Koma kuli Mulungu kumwamba amene ndi Woulula zinsinsi,+ ndipo wakudziwitsani, inu Mfumu Nebukadinezara, zimene zidzachitike m’masiku otsiriza.+ Maloto anu ndi masomphenya amene munaona muli pabedi lanu ndi awa:
29 “Inu mfumu, mutagona pabedi lanu,+ munayamba kuganiza za zimene zidzachitike m’tsogolo, ndipo Mulungu amene ndi Woulula zinsinsi wakudziwitsani zimene zidzachitike.+ 30 Sikuti chinsinsi chimenechi chaululidwa kwa ine chifukwa chakuti ndine wanzeru kuposa munthu wina aliyense ayi,+ koma chaululidwa ndi cholinga chakuti ndikumasulireni malotowo mfumu, ndiponso kuti mudziwe maganizo a mumtima mwanu.+
31 “Inuyo mfumu munaona chifaniziro chinachake chachikulu kwambiri. Chifaniziro chimenechi chinali chitaima patsogolo panu ndipo maonekedwe ake anali ochititsa mantha. Chinali chachikulu ndiponso chowala modabwitsa. 32 Mutu wa chifaniziro chimenechi unali wopangidwa ndi golide wabwino,+ chifuwa chake ndi manja ake zinali zasiliva,+ mimba yake ndi ntchafu zake zinali zamkuwa,+ 33 miyendo yake inali yachitsulo,+ ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanizika ndi dongo.+ 34 Munapitiriza kuchiyang’ana kufikira mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu.+ Mwalawo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanizika ndi dongo ndipo unawapera.+ 35 Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide, zonsezi zinaphwanyikaphwanyika ndipo zinakhala ngati mankhusu* apamalo opunthirapo mbewu+ m’chilimwe. Mphepo inaziuluza moti sizinaonekenso.+ Koma mwala umene unamenya chifanizirocho unakhala phiri lalikulu ndipo linadzaza dziko lonse lapansi.+
36 “Maloto anu ndi amenewa ndipo kumasulira kwake tikuuzani mfumu.+ 37 Inuyo mfumu, mfumu ya mafumu, inu amene Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu,+ mphamvu, ndi ulemerero, 38 inuyo amene Mulungu wakupatsani+ nyama zakutchire ndi mbalame zam’mlengalenga kulikonse kumene kuli anthu, amene Mulungu wakuikani kukhala wolamulira zonsezo, inuyo ndiye mutu wagolide.+
39 “Pambuyo panu padzabwera ufumu wina+ wotsikirapo kwa inu.+ Kenako padzabweranso ufumu wina wachitatu, wamkuwa, umene udzalamulira dziko lonse lapansi.+
40 “Ufumu wachinayi+ udzakhala wolimba ngati chitsulo.+ Popeza kuti chitsulo chimaphwanya ndi kupera china chilichonse, ufumuwo udzaphwanya ndi kuswa maufumu ena onsewa mofanana ndi chitsulo chimene chimaswa zinthu.+
41 “Popeza munaona kuti mapazi ndi zala zakumiyendo zinali zadongo la woumba mbiya losakanizika ndi chitsulo,+ ufumuwo udzakhala wogawanika,+ koma udzakhala wolimba pa zinthu zina ngati chitsulo. Zimenezi zili choncho chifukwa munaona kuti chitsulocho chinali chosakanizika ndi dongo lonyowa.+ 42 Popeza zala zakumiyendo zinali zachitsulo chosakanizika ndi dongo, pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba. 43 Popeza munaona chitsulo chosakanizika ndi dongo lonyowa, mbali zake zina zidzasakanizika ndi ana a anthu koma sadzagwirizana monga mmene zilili zosatheka kuti chitsulo chisakanizike bwinobwino ndi dongo.
44 “M’masiku a mafumu amenewo,+ Mulungu wakumwamba+ adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.+ Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu,+ koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo,+ ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.+ 45 Zidzakhala choncho chifukwa munaona kuti mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu,+ ndipo unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide.+ Inu mfumu, Mulungu Wamkulu+ wakudziwitsani zimene zidzachitike m’tsogolo.+ Maloto amenewa ndi odalirika ndipo kumasulira kwake ndi kokhulupirika.”+
46 Pamenepo Mfumu Nebukadinezara anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anapereka ulemu kwa Danieli. Iye analamulanso kuti Danieli apatsidwe mphatso ndipo amufukizire zofukiza zonunkhira.+ 47 Mfumuyo inauza Danieli kuti: “Ndithudi Mulungu wa anthu inu ndi Mulungu wa milungu yonse,+ Ambuye wa mafumu onse+ ndiponso Woulula zinsinsi, chifukwa iwe wakwanitsa kuulula chinsinsi chimenechi.”+ 48 Pa chifukwa chimenechi, mfumu inamukweza pa udindo Danieli+ ndipo inamupatsa mphatso zambiri. Inamuikanso kukhala wolamulira chigawo chonse cha Babulo+ ndiponso wamkulu wa akuluakulu a boma* oyang’anira amuna onse anzeru a m’Babulo. 49 Ndipo Danieli anapempha mfumu kuti iike Sadirake, Mesake ndi Abedinego+ kuti akhale oyang’anira chigawo cha Babulo, ndipo mfumuyo inawaikadi. Koma Danieli anali kutumikira m’nyumba ya mfumu.+
3 Nebukadinezara anapanga fano lagolide.+ Fanoli linali lalitali mikono* 60 ndipo m’lifupi mwake linali mikono 6. Analiimika m’chigwa cha Dura, m’chigawo cha Babulo.+ 2 Nebukadinezara monga mfumu anatumiza uthenga kwa masatarapi,* akuluakulu a boma,*+ abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu apolisi+ ndi oyang’anira onse a zigawo kuti asonkhane ku mwambo wotsegulira+ fano limene mfumu Nebukadinezara inaimika.
3 Pa nthawi imeneyo masatarapi,+ akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu apolisi ndi oyang’anira onse a zigawo, anasonkhana ku mwambo wotsegulira fano limene mfumu Nebukadinezara inaimika. Iwo anaimirira patsogolo pa fano limene Nebukadinezara anaimikalo. 4 Tsopano wolengeza mauthenga+ anayamba kufuula kuti: “Tamverani inu anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana.+ 5 Mukangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ mugwade ndi kuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndi kulambira fano lagolide limene mfumu Nebukadinezara yaimika. 6 Aliyense amene sagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kulambira fanolo,+ nthawi yomweyo+ aponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto.”+ 7 Chifukwa cha mawu amenewa, patangomveka kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira, anthu onse a mitundu yosiyanasiyana,+ olankhula zinenero zosiyanasiyana, anagwada mpaka nkhope zawo pansi ndi kulambira fano lagolide limene mfumu Nebukadinezara inaimika.
8 Nthawi yomweyo, Akasidi* ena anapita kwa mfumu kukaneneza Ayuda.+ 9 Iwo anauza mfumu Nebukadinezara kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale.+ 10 Inuyo mfumu munaika lamulo lakuti munthu aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ agwade ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndipo alambire fano lagolide. 11 Munalamulanso kuti aliyense amene sagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi n’kulambira fanolo aponyedwe m’ng’anjo yoyaka moto.+ 12 Koma pali Ayuda ena amene munawaika kukhala oyang’anira chigawo cha Babulo.+ Amuna amphamvu amenewa, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, sakukumverani inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu ndipo sakulambira fano lagolide limene mwaimika.”+
13 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri+ ndipo analamula kuti abweretse Sadirake, Mesake ndi Abedinego.+ Choncho anabweretsadi amuna amphamvu amenewa pamaso pa mfumu. 14 Ndiyeno Nebukadinezara anawafunsa kuti: “Kodi ndi zoonadi kuti inu Sadirake, Mesake ndi Abedinego simukutumikira milungu yanga+ ndi kulambira fano lagolide limene ndaimika?+ 15 Tsopano ngati mwakonzeka kuti mukamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ mugwada n’kuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndi kulambira fano lagolide, zili bwino. Koma ngati simulilambira, nthawi yomweyo muponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto. Ndipo ndi mulungu uti amene angakupulumutseni m’manja mwanga?”+
16 Pamenepo Sadirake, Mesake ndi Abedinego anayankha mfumuyo kuti: “Inu mfumu Nebukadinezara, palibenso chimene ife tinganene kwa inu pa nkhani imeneyi.+ 17 Ngati mungatiponyere m’ng’anjo yoyaka moto, Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa. Iye atipulumutsa m’ng’anjo yoyaka moto ndiponso m’manja mwanu mfumu.+ 18 Koma ngati satipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sititumikira milungu yanu, ndipo sitilambira fano limene mwaimika.”+
19 Pamenepo Nebukadinezara anapsera mtima Sadirake, Mesake ndi Abedinego ndipo nkhope yake inasintha. Iye analamula kuti ng’anjoyo aisonkhezere kuwirikiza ka 7 kuposa mmene anali kuchitira nthawi zonse. 20 Iye anauza asilikali ake ena amphamvu+ kuti amange Sadirake, Mesake ndi Abedinego ndi kuwaponya m’ng’anjo yoyaka motoyo.+
21 Chotero amuna amphamvuwa anamangidwa atavala nsalu zawo zakunja, zovala zawo, zisoti zawo ndi zovala zawo zina zonse ndipo anawaponya m’ng’anjo yoyaka motoyo. 22 Koma chifukwa chakuti mfumu inalamula zimenezi itapsa mtima kwambiri ndipo ng’anjo ya moto anaisonkhezera mopitirira muyezo, asilikali amphamvu amene anatenga Sadirake, Mesake ndi Abedinego aja ndi amene anaphedwa ndi malawi a moto. 23 Ndipo amuna ena amphamvuwa, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, anagwera pakatikati pa ng’anjo yoyaka moto.+
24 Pamenepo, mfumu Nebukadinezara anachita mantha kwambiri ndipo ananyamuka mwachangu. Iye anauza nduna zake zapamwamba kuti: “Kodi sitinaponye amuna atatu amphamvu pakati pa moto titawamanga?”+ Ndunazo zinamuyankha kuti: “Inde, mfumu.” 25 Ndiyeno mfumu inati: “Taonani! Inetu ndikuona amuna amphamvu anayi akuyendayenda pakati pa moto osapsa, ndipo munthu wachinayiyo akuoneka ngati mulungu.”+
26 Kenako Nebukadinezara anayandikira khomo la ng’anjo yoyaka motoyo+ ndipo anati: “Sadirake, Mesake ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wam’mwambamwamba,+ tulukani ndipo mubwere kuno!” Zitatero, Sadirake, Mesake ndi Abedinego anatuluka pakati pa motopo. 27 Tsopano masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa, ndi nduna zapamwamba+ za mfumu zimene zinasonkhana zinaonadi kuti motowo sunavulaze amuna amphamvu amenewa,+ ndipo tsitsi lawo silinawauke ndi limodzi lomwe.+ Zovala zawo sizinasinthe ndipo sanali kumveka ngakhale fungo la moto.
28 Pamenepo Nebukadinezara anati: “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesake ndi Abedinego+ amene anatumiza mngelo wake+ ndi kupulumutsa atumiki ake amene anamudalira+ ndiponso amene sanamvere mawu a mfumu, koma anali okonzeka kufa chifukwa sanafune kutumikira+ ndi kulambira+ mulungu wina aliyense kupatulapo Mulungu wawo.+ 29 Tsopano ine ndikuika lamulo+ lakuti, anthu onse a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana amene anganene chilichonse chotsutsana ndi Mulungu wa Sadirake, Mesake ndi Abedinego ayenera kudulidwa nthulinthuli,+ ndipo nyumba zawo zisandutsidwe zimbudzi za anthu onse,+ pakuti palibe mulungu wina amene amatha kupulumutsa chotere.”+
30 Pamenepo mfumu inachititsa kuti Sadirake, Mesake ndi Abedinego zinthu ziziwayendera bwino m’chigawo cha Babulo.+
4 “Uwu ndi uthenga wochokera kwa ine mfumu Nebukadinezara wopita kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana amene akukhala padziko lonse lapansi:+ Mukhale ndi mtendere wochuluka.+ 2 Ndaona kuti n’kwabwino kuti ndikuuzeni+ zizindikiro ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wam’mwambamwamba wandichitira. 3 Zizindikiro zake n’zazikulu ndipo zodabwitsa zake n’zamphamvu.+ Ufumu wake udzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo ulamuliro wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
4 “Ine Nebukadinezara ndinali kukhala mosatekeseka+ m’nyumba mwanga ndipo zinthu zinali kundiyendera bwino m’nyumba yanga yachifumu.+ 5 Kenako ndinalota maloto amene anayamba kundichititsa mantha.+ Ndili pabedi langa ndinaona zithunzithunzi ndi masomphenya m’maganizo mwanga. Zimenezi zinayamba kundichititsa mantha.+ 6 Pamenepo ndinalamula kuti amuna onse anzeru a m’Babulo abwere kwa ine kuti adzandimasulire malotowo.+
7 “Chotero ansembe ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi*+ ndi okhulupirira nyenyezi+ anabwera kwa ine ndipo ndinawauza malotowo, koma iwo sanathe kuwamasulira.+ 8 Kenako Danieli, amene ndinamupatsa dzina lakuti Belitesazara+ pofuna kulemekeza mulungu wanga,+ amenenso mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera,+ anabwera kwa ine ndipo ndinamuuza malotowo. Ndinati:
9 “‘Iwe Belitesazara mkulu wa ansembe ochita zamatsenga,+ ndikudziwa bwino kuti mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe+ ndipo palibe chinsinsi chimene umavutika nacho.+ Chotero ndiuze zimene ndinaona m’maloto anga ndi kumasulira kwake.+
10 “‘Ine ndinaona masomphenya nditagona pabedi langa.+ Ndinaona mtengo+ wautali kwambiri+ uli pakati pa dziko lapansi. 11 Mtengowo unakula ndipo unakhala wamphamvu kwambiri. Unatalika mpaka kufika kumwamba ndipo unali kuonekera ngakhale kumalekezero a dziko lonse lapansi.+ 12 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira chamoyo chilichonse. Nyama zakutchire+ zinali kukhala mumthunzi wake.+ Mbalame zam’mlengalenga zinali kukhala panthambi zake+ ndipo zamoyo zonse zinali kupeza chakudya mmenemo.
13 “‘Nditagona pabedi langa, ndinapitiriza kuona masomphenya ndipo ndinangoona mlonda+ woyera+ akutsika kuchokera kumwamba. 14 Mlondayo anali kulankhula mofuula kuti: “Gwetsani mtengowo+ ndipo dulani nthambi zake. Yoyolani masamba ake ndi kumwaza zipatso zake. Nyama zithawe pansi pake ndipo mbalame zichoke panthambi zake,+ 15 koma musiye chitsa chake munthaka. Chitsacho muchikulunge ndi mkombero wachitsulo ndi wamkuwa. Chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba. Chikhalenso pakati pa nyama zakutchire ndi udzu wa padziko lapansi.+ 16 Mtima wake usinthidwe kuchoka kumtima wa munthu n’kukhala mtima wa nyama+ ndipo padutse nthawi zokwanira 7.+ 17 Alonda+ ndi amene alamula zimenezi. Angelo oyera* ndi amene apempha zimenezi ndi cholinga chakuti anthu adziwe kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu,+ ndiponso adziwe kuti iye akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa+ ndipo amaika ngakhale munthu wonyozeka kwambiri kuti azilamulira.”+
18 “‘Amenewa ndiwo maloto amene ine Mfumu Nebukadinezara ndinalota. Tsopano iwe Belitesazara umasulire malotowa, pakuti amuna ena onse anzeru a mu ufumu wanga alephera kuwamasulira.+ Koma iwe ungathe kuwamasulira chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.’+
19 “Pa nthawi imeneyo Danieli, wotchedwa Belitesazara,+ anada nkhawa kwa kanthawi ndipo anachita mantha.+
“Chotero mfumuyo inamuuza kuti, ‘Iwe Belitesazara, malotowa ndi kumasulira kwake zisakuchititse mantha.’+
“Belitesazara anayankha kuti, ‘Inu mbuyanga, zikanakhala bwino malotowa akanakhala okhudza anthu amene amadana nanu. Zikanakhalanso bwino kumasulira kwake kukanakhala kokhudza adani anu.+
20 “‘Inu munaona mtengo umene unakula kwambiri ndipo unakhala wamphamvu kwambiri. Mtengowo unatalika mpaka kufika kumwamba ndipo unali kuoneka padziko lonse lapansi.+ 21 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira chamoyo chilichonse. Nyama zakutchire zinali kukhala pansi pake.+ Mbalame zam’mlengalenga zinali kukhala panthambi zake. 22 Mtengowo ndinuyo mfumu,+ chifukwa mwakula ndipo mwakhala ndi mphamvu. Ulemerero wanu wakula mpaka kufika kumwamba+ ndipo ulamuliro wanu wafika kumalekezero a dziko lapansi.+
23 “‘Chifukwa chakuti inu mfumu munaona mlonda woyera+ akutsika kuchokera kumwamba, akunena kuti: “Gwetsani mtengowo ndipo muuwononge, koma musiye chitsa chake munthaka, mutachikulunga ndi mkombero wachitsulo ndi wamkuwa, chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba, chikhale limodzi ndi nyama zakutchire kufikira patadutsa nthawi zokwanira 7,”+ 24 lamulo+ la Wam’mwambamwamba+ ligwera inu mbuyanga mfumu,+ ndipo kumasulira kwake ndi uku: 25 Inuyo adzakuthamangitsani pakati pa anthu ndipo muzidzakhala pakati pa nyama zakutchire.+ Muzidzadya udzu ngati ng’ombe+ ndipo muzidzanyowa ndi mame akumwamba. Ndiyeno padzadutsa nthawi zokwanira 7+ kufikira mutadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu,+ ndiponso kuti akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.+
26 “‘Popeza ananena kuti asiye chitsa cha mtengowo,+ inu mudzayambiranso kulamulira mu ufumu wanu mutadziwa kuti Mulungu ndiye akulamulira kumwamba.+ 27 Chotero inu mfumu, chonde mverani malangizo anga+ ndipo chotsani machimo anu pochita zolungama.+ Muchotsenso zolakwa zanu pochitira chifundo osauka.+ Mukatero, mwina zinthu zidzapitiriza kukuyenderani bwino kwa nthawi yaitali.’”+
28 Zonsezi zinagweradi mfumu Nebukadinezara.+
29 Patapita miyezi 12 kuchokera pamene analota maloto amenewa, Nebukadinezarayo anali kuyenda padenga* la nyumba yachifumu ya ku Babulo. 30 Mfumuyo inali kunena kuti:+ “Kodi uyu si Babulo Wamkulu amene ine ndamanga ndi mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso ndi ulemerero wanga waukulu ndi cholinga chakuti kukhale nyumba yachifumu?”+
31 Mfumuyo ili mkati molankhula mawu amenewa, kumwamba kunamveka mawu akuti: “Tamvera iwe mfumu Nebukadinezara! ‘Ufumu wachoka m’manja mwako,+ 32 ndipo akuthamangitsa pakati pa anthu. Uyamba kukhala pakati pa nyama zakutchire+ ndipo uzidzadya udzu ngati ng’ombe. Ndiyeno padutsa nthawi zokwanira 7 kufikira utadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.’”+
33 Nthawi yomweyo+ mawuwa anakwaniritsidwa pa Nebukadinezara ndipo anathamangitsidwa pakati pa anthu. Iye anayamba kudya udzu ngati ng’ombe ndipo thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba. Tsitsi lake linatalika kwambiri ngati nthenga za chiwombankhanga ndipo zikhadabo zake zinatalika ngati za mbalame.+
34 “Pamapeto pa masiku amenewa,+ ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba+ ndipo nzeru zanga zinayamba kubwerera. Ndinatamanda Wam’mwambamwamba+ ndipo amene adzakhalapo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza,+ chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+ 35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
36 “Ndiyeno kuti ndipezenso ulemerero wa ufumu wanga, ukulu ndi nzeru zanga zinayamba kubwerera kwa ine.+ Pamenepo alangizi anga ndi nduna zanga anayamba kufunsiranso malangizo anga. Kenako ndinabwezeretsedwa pampando wanga wachifumu ndipo anthu anayamba kundipatsa ulemu waukulu.+
37 “Tsopano ine Nebukadinezara ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba,+ chifukwa ntchito zake zonse ndizo choonadi, njira zake ndi zolungama,+ ndiponso amatha kutsitsa anthu onyada.”+
5 Ndiyeno mfumu Belisazara+ anakonzera nduna zake 1,000 phwando lalikulu, ndipo iyeyo anali kumwa vinyo+ atakhala kutsogolo kwawo. 2 Belisazara ataledzera ndi vinyoyo+ anaitanitsa ziwiya zagolide ndi zasiliva+ zimene Nebukadinezara bambo ake anatenga m’kachisi ku Yerusalemu. Anaitanitsa zimenezi kuti mfumuyo, nduna zake, adzakazi* ake ndi akazi ake ena apambali amweremo.+ 3 Pa nthawi imeneyo anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga m’kachisi, m’nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenako mfumuyo, nduna zake, adzakazi ake ndi akazi ake ena apambali anayamba kumwera m’ziwiyazo. 4 Pakumwa vinyoyo, iwo anali kutamanda milungu yagolide, yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala.+
5 Pamene anali kuchita zimenezi, zala za munthu zinaonekera ndipo zinayamba kulemba pafupi ndi choikapo nyale, papulasitala wa pakhoma* la nyumba ya mfumu,+ ndipo mfumuyo inaona dzanja limene linali kulembalo. 6 Pa nthawi imeneyo nkhope ya mfumuyo inasintha ndipo inachita mantha.+ Miyendo yake inafooka+ ndipo mawondo ake anayamba kunjenjemera.+
7 Ndiyeno mfumuyo inafuula kuti aibweretsere olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi.+ Mfumuyo inauza amuna anzeru a m’Babulo amenewa kuti: “Aliyense amene angawerenge mawuwa ndi kundiuza kumasulira kwake, ndimuveka zovala zofiirira*+ ndi mkanda wagolide m’khosi, ndipo ndimuika kukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+
8 Pa nthawi imeneyo amuna onse anzeru anabwera kwa mfumu koma sanathe kuwerenga mawu olembedwawo kapena kuiuza mfumu kumasulira kwake.+ 9 Chotero Mfumu Belisazara inachita mantha kwambiri ndipo nkhope yake inasintha. Nduna zakenso zinathedwa nzeru.+
10 Tsopano popeza mfumukazi inamva mawu a mfumu ndi a nduna zake, inalowa m’chipinda chimene anali kuchitira phwandolo. Mfumukaziyo inati: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale.+ Musachite mantha komanso nkhope yanu isasinthe. 11 Mu ufumu wanu muli munthu amene ali ndi mzimu wa milungu yoyera.+ M’masiku a bambo anu, anthu anazindikira kuti munthuyu ndi wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndiponso ali ndi nzeru zofanana ndi nzeru za milungu. Chotero bambo anu, Mfumu Nebukadinezara, anamuika kukhala mkulu+ wa ansembe ochita zamatsenga, anthu okhulupirira mizimu, Akasidi ndi anthu okhulupirira nyenyezi. Ndithudi mfumu, bambo anu anamupatsa udindo umenewu. 12 Anachita zimenezi chifukwa munthuyu anali ndi luso lodabwitsa, anali wodziwa zinthu ndi wozindikira pa nkhani yomasulira maloto,+ kumasulira mikuluwiko ndi kumasula mfundo. Zinthu zonsezi zinapezeka mwa munthu ameneyu+ Danieli, amene mfumu inamupatsa dzina lakuti Belitesazara.+ Tsopano itanani Danieli kuti adzakuuzeni kumasulira kwa zolembedwazi.”
13 Choncho anabweretsa Danieli kwa mfumu, ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe Danieli, mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda+ ndi bambo anga mfumu?+ 14 Ndamva kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu+ ndiponso kuti ndiwe wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndi wanzeru+ zodabwitsa. 15 Tsopano ineyo anandibweretsera amuna anzeru ndi anthu okhulupirira mizimu kuti awerenge zolembedwazi ndi kundiuza kumasulira kwake, koma iwo alephera kumasulira mawuwa.+ 16 Ndamvanso kuti iweyo umatha kumasulira zinthu+ ndi kumasula mfundo. Tsopano ngati ungathe kuwerenga mawuwa ndi kundiuza kumasulira kwake, ndikuveka zovala zofiirira ndi mkanda wagolide m’khosi, ndipo ndikuika kukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+
17 Pamenepo Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Sungani mphatso zanuzo ndipo mphoto zanuzo mupatse ena.+ Komabe, ndikuwerengerani zolembedwazi ndipo ndikuuzani kumasulira kwake.+ 18 Inu mfumu, Mulungu Wam’mwambamwamba+ anapatsa bambo anu+ Nebukadinezara ufumu, ukulu, ulemu ndi ulemerero.+ 19 Chifukwa chakuti Mulungu anamupatsa ukulu umenewu, anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana anali kunjenjemera ndi kuchita mantha pamaso pake.+ Iye akafuna kupha munthu aliyense anali kumupha, akafuna kuwononga munthu aliyense anali kumuwononga, akafuna kukweza munthu aliyense anali kumukweza ndipo akafuna kutsitsa munthu aliyense anali kumutsitsa.+ 20 Koma pamene mtima wake unayamba kudzitukumula ndiponso pamene anaumitsa mtima wake ndi kuchita zinthu modzikweza,+ anatsitsidwa pampando wake wachifumu ndipo ulemerero wake unachotsedwa.+ 21 Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo mtima wake unasinthidwa n’kukhala ngati wa nyama. Anayamba kukhala limodzi ndi abulu akutchire+ ndipo anali kudya udzu ngati ng’ombe. Thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba,+ kufikira pamene anadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kuika munthu aliyense kuti akhale wolamulira, amamuika.+
22 “Koma inuyo a Belisazara,+ amene ndinu mwana wake, simunadzichepetse mumtima mwanu+ ngakhale kuti munali kudziwa zonsezi.+ 23 Mwadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba+ ndipo anthu akubweretserani ziwiya za m’nyumba yake.+ Inuyo, nduna zanu, adzakazi anu ndi akazi anu ena apambali mwamwera vinyo m’ziwiya zimenezi. Mwatamanda milungu wamba yasiliva, yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala+ imene siona, kumva kapena kudziwa kalikonse.+ Koma Mulungu amene amasunga mpweya wanu+ ndi njira zanu zonse m’dzanja lake,+ simunamulemekeze.+ 24 Chotero Mulungu watumiza dzanja ndipo wachititsa kuti mawu amenewa alembedwe.+ 25 Mawu amene alembedwa ndi awa: MENE, MENE, TEKELI, ndi PARASINI.
26 “Kumasulira kwa mawuwa ndi uku: MENE, Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu ndipo waumaliza.+
27 “TEKELI, mwayezedwa pasikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera.+
28 “PERESI,* ufumu wanu wagawanika ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+
29 Pamenepo Belisazara analamula kuti Danieli amuveke zovala zofiirira ndi mkanda wagolide m’khosi mwake, ndipo analengeza kuti Danieli akhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.+
30 Usiku womwewo, Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa,+ 31 ndipo Dariyo+ Mmedi anapatsidwa ufumuwo ali ndi zaka pafupifupi 62.
6 Ndiyeno Dariyo anaona kuti ndi bwino kuti aike masatarapi* 120 oyang’anira zigawo zonse za ufumu wake.+ 2 Anaikanso nduna zapamwamba zitatu zoyang’anira masatarapiwo, ndipo Danieli anali mmodzi wa ndunazo.+ Anaika nduna zimenezi kuti nthawi zonse masatarapiwo+ aziziuza chilichonse chimene chikuchitika, ndi cholinga chakuti zinthu za mfumu zisawonongeke.+ 3 M’kupita kwa nthawi, Danieli anaonetsa kuti anali wodziwa kugwira ntchito bwino+ kuposa nduna zonse zapamwamba ndi masatarapi onse, chifukwa anali ndi luso lodabwitsa+ ndipo mfumu inali kuganiza zomukweza kuti akhale pamwamba pa wina aliyense mu ufumuwo.
4 Poona zimenezi, nduna zapamwamba ndi masatarapi aja nthawi zonse anali kufunafuna chomunamizira Danieli pa kayendetsedwe kake ka zinthu mu ufumuwo.+ Koma iwo sanapeze chifukwa chilichonse chomunamizira kapena chinthu chilichonse chachinyengo chimene anachita, pakuti iye anali wokhulupirika. Iwo anapeza kuti Danieli sanali kunyalanyaza kanthu kapena kuchita zachinyengo zilizonse.+ 5 Chotero amuna amphamvuwa anati: “Danieliyu sitingamupezere chifukwa chilichonse. Ngati tikufuna kumupezera chifukwa, chikhale chokhudzana ndi lamulo la Mulungu wake.”+
6 Choncho nduna zapamwamba zimenezi ndi masatarapi aja anapita kwa mfumu ali chigulu.+ Iwo anauza mfumuyo kuti: “Inu mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo mpaka kalekale.+ 7 Nduna zonse zapamwamba za mu ufumu uno, akuluakulu a boma, masatarapi, alangizi a mfumu, ndi abwanamkubwa agwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo+ loletsa munthu aliyense kupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense kwa masiku 30, kupatulapo kwa inu nokha mfumu. Aliyense amene samvera lamulo limeneli aponyedwe m’dzenje la mikango.+ 8 Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo ndipo musaine+ kuti lamulolo lisasinthe, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya,+ amene sasintha.”+
9 Mogwirizana ndi zimenezi, Mfumu Dariyo inasainira lamulolo.+
10 Koma Danieli atangodziwa kuti lamulo limeneli lasainidwa, analowa m’nyumba mwake, ndipo mawindo a nyumba yake oyang’ana ku Yerusalemu+ anali otsegula. M’nyumbamo, iye anali kugwada ndi kupemphera+ kwa Mulungu wake ndi kumutamanda+ katatu pa tsiku,+ monga mmene anali kuchitira nthawi zonse lamuloli lisanasainidwe.+ 11 Nthawi yomweyo, amuna amphamvu amenewa analowa m’nyumbamo ali chigulu ndipo anapeza Danieli akuchonderera ndi kupempha Mulungu wake kuti amukomere mtima.+
12 Kenako anapita kwa mfumu ndi kuifunsa za lamulo limene inakhazikitsa lija, kuti: “Kodi inu mfumu, si paja mwakhazikitsa lamulo lonena kuti kwa masiku 30 munthu aliyense wopezeka akupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense, kupatulapo kwa inu nokha, aponyedwe m’dzenje la mikango?”+ Mfumuyo inayankha kuti: “Nkhani imeneyi ndi yodziwika bwino, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya, amene sasintha.”+ 13 Nthawi yomweyo iwo anauza mfumuyo kuti: “Danieli,+ mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda,+ sanakumvereni mfumu komanso sanamvere lamulo limene munasainira ndipo akupemphera katatu pa tsiku.”+ 14 Mfumuyo itangomva mawu amenewa, inakhumudwa kwambiri+ ndipo inayamba kuganiza za mmene ingapulumutsire Danieli.+ Inakhala ikufunafuna njira yomupulumutsira mpaka dzuwa linalowa. 15 Pamapeto pake, amuna amphamvu amenewa anapita kwa mfumu ali chigulu ndipo anaiuza kuti: “Inu mfumu, mukudziwa kuti malamulo a Amedi ndi Aperisiya amanena kuti lamulo lililonse+ lokhazikitsidwa ndi mfumu siliyenera kusinthidwa.”+
16 Zitatero mfumuyo inalamula kuti abweretse Danieli. Atabwera naye anamuponya m’dzenje la mikango.+ Koma mfumu inauza Danieli kuti: “Mulungu wako amene umamutumikira mosalekeza akupulumutsa.”+ 17 Ndiyeno anabweretsa mwala ndi kutseka pakhomo la dzenjelo. Kenako mfumu inadinda mwalawo ndi mphete yake yodindira ndipo nduna zakenso zinaudinda ndi mphete yawo yodindira, kuti chilichonse chokhudza Danieli chisasinthidwe.+
18 Kenako mfumu inapita kunyumba yake yachifumu. Usiku umenewo mfumuyo inasala kudya+ ndipo sanaiimbire nyimbo ndi zipangizo zoimbira, komanso sinathe kugona tulo.+ 19 Ndiyeno kutangoyamba kuwala m’bandakucha, mfumuyo inadzuka ndipo inapita mofulumira kudzenje la mikango lija. 20 Itayandikira dzenjelo, inafuulira Danieli ndi mawu achisoni kuti: “Danieli mtumiki wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako amene umamutumikira mosalekeza+ wakupulumutsa kwa mikango?”+ 21 Nthawi yomweyo Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 22 Mulungu wanga+ watumiza mngelo wake+ kudzatseka pakamwa pa mikango.+ Chotero mikangoyo sinandivulaze, chifukwa iye sanandipeze ndi mlandu uliwonse+ ndiponso sindinakulakwireni chilichonse inu mfumu.”+
23 Pamenepo mfumuyo inasangalala kwambiri+ ndipo inalamula kuti Danieli amutulutse m’dzenjemo. Danieli anatulutsidwadi m’dzenjelo ndipo sanavulale paliponse chifukwa anakhulupirira Mulungu wake.+
24 Zitatero, mfumu inalamula kuti abweretse amuna amphamvu amene ananenera Danieli zoipa aja,+ ndipo anawabweretsadi. Kenako anawaponya m’dzenje la mikango+ pamodzi ndi ana awo ndi akazi awo.+ Iwo asanafike n’komwe pansi pa dzenjelo, mikango inawakhadzulakhadzula ndi kuphwanya mafupa awo onse.+
25 Ndiyeno mfumu Dariyo inalemba makalata opita kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndi anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana okhala padziko lonse lapansi,+ kuti: “Mukhale ndi mtendere wochuluka.+ 26 Ine ndikulamula+ kuti m’zigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera ndi kuchita mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Pakuti iye ndi Mulungu wamoyo, amene adzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo ufumu wake+ sudzawonongeka+ komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+ 27 Iye amapulumutsa ndi kulanditsa anthu ake,+ ndipo amachita zizindikiro komanso zinthu zodabwitsa kumwamba+ ndi padziko lapansi,+ moti wapulumutsa Danieli kwa mikango.”
28 Choncho zinthu zinamuyendera bwino Danieli mu ufumu wa Dariyo+ ndiponso mu ufumu wa Koresi Mperisiya.+
7 M’chaka choyamba cha ulamuliro wa Belisazara+ mfumu ya Babulo, Danieli analota maloto ndipo anaona masomphenya atagona pabedi lake.+ Pa nthawi imeneyo, analemba zimene analotazo,+ ndipo anafotokoza nkhani yonseyo. 2 Iye anati:
“M’masomphenya ausiku, ndinaona mphepo zinayi+ zakumwamba zikuvundula nyanja yaikulu.+ 3 Zilombo zinayi zikuluzikulu+ zinali kutuluka m’nyanjayo,+ ndipo chilichonse chinali chosiyana ndi chinzake.+
4 “Chilombo choyamba chinali chooneka ngati mkango+ ndipo chinali ndi mapiko a chiwombankhanga.+ Ndinapitiriza kuchiyang’ana kufikira pamene mapiko ake anathotholedwa. Ndiyeno anachitukula padziko lapansi+ ndipo anachiimiritsa ndi miyendo iwiri ngati munthu. Kenako chinapatsidwa mtima wa munthu.+
5 “Ndinaonanso chilombo china chachiwiri, chooneka ngati chimbalangondo.+ Chinali chotukuka mbali imodzi+ ndipo m’kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake. Chilombochi chinauzidwa kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri.’+
6 “Pambuyo pa zimenezi, ndinaona chilombo china chooneka ngati kambuku*+ koma chinali ndi mapiko anayi a mbalame pamsana pake. Chilombochi chinali ndi mitu inayi+ ndipo chinapatsidwa ulamuliro.
7 “Kenako ndinaonanso m’masomphenya ausiku chilombo chachinayi, choopsa kwambiri ndiponso chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri.+ Chinali ndi mano akuluakulu achitsulo ndipo chinali kudya ndi kuphwanyaphwanya chilichonse chimene chinali nacho pafupi. Zotsala chinali kuzipondaponda ndi mapazi ake. Chinali chosiyana ndi zilombo zina zonse zimene ndinaona poyamba ndipo chinali ndi nyanga 10.+ 8 Pamene ndinali kuyang’anitsitsa nyangazo, ndinaona kuti nyanga ina yaing’ono yamera+ pakati pa nyangazo. Nyanga zitatu pa nyangazi zinazulidwa pamalo amene nyanga yaing’onoyo inamera. Nyangayi inali ndi maso ngati a munthu, ndipo inali ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula.+
9 “Ndiyeno ndinapitiriza kuyang’ana kufikira pamene mipando yachifumu inaikidwa+ ndipo Wamasiku Ambiri+ anakhala pa mpando wake wachifumu. Zovala zake zinali zoyera kwambiri.+ Tsitsi lake linali looneka ngati ubweya wa nkhosa woyera.+ Mpando wake wachifumu unali kuyaka moto walawilawi,+ ndipo mawilo a mpandowo anali kuyaka moto.+ 10 Mtsinje wa moto unali kuyenda kuchokera kwa iye.+ Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse,+ ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.+ Bwalo la milandu+ linakhala pansi, ndipo mabuku anatsegulidwa.
11 “Pa nthawi imeneyo, ndinapitirizabe kuyang’ana chifukwa ndinali kumva mawu odzitukumula amene nyanga ija inali kulankhula.+ Ndinapitirizanso kuyang’ana kufikira pamene chilombocho chinaphedwa ndipo thupi lake linaponyedwa pamoto n’kuwonongedwa.+ 12 Koma zilombo zinazo+ anazilanda ulamuliro, ndipo anazilola kukhalapo kwa kanthawi.+
13 “Ndiyeno m’masomphenya ausikuwo, ndinaonanso wina wooneka ngati mwana wa munthu+ akubwera m’mitambo.+ Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri uja,+ ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Iye.+ 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+
15 “Tsopano ineyo Danieli, ndinavutika kwambiri mumtima chifukwa cha zimenezi ndipo ndinachita mantha ndi masomphenya amene ndinaona.+ 16 Ndinayandikira mmodzi mwa amene anali ataimirira kuti ndimufunse tanthauzo la zonsezi.+ Choncho iye anandifotokozera kumasulira kwa nkhani zimenezi, kuti:
17 “‘Popeza zilombo zikuluzikulu zimenezi zilipo zinayi,+ pali mafumu anayi amene adzauka padziko lapansi.+ 18 Koma oyera+ a Wamkulukulu+ adzalandira ufumu ndipo adzatenga ufumuwo+ mpaka kalekale, ku nthawi zosatha.’
19 “Ndiyeno ndinali ndi chidwi chofuna kudziwa zambiri zokhudza chilombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zina zonse. Chilombo chimenechi chinali choopsa kwambiri. Mano ake anali achitsulo, zikhadabo zake zinali zamkuwa, ndipo chinali kudya zinthu ndi kuziphwanyaphwanya. Zotsala chinali kuzipondaponda ndi mapazi ake.+ 20 Ndinafunanso kudziwa za nyanga 10 zimene zinali pamutu pake+ ndi nyanga ina+ imene inamera, imene inachititsa kuti nyanga zitatu zigwe.+ Nyanga imeneyi inali ndi maso ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula+ ndipo inali kuoneka yaikulu kuposa zinzake zija.
21 “Ndinapitirizabe kuyang’ana pamene nyangayo inathira nkhondo pa oyera ndipo inali kuwagonjetsa,+ 22 kufikira Wamasiku Ambiri+ anabwera ndipo anapereka chiweruzo chokomera oyera a Wamkulukulu.+ Tsopano nthawi yoti oyerawo atenge ufumuwo inakwana, ndipo anautengadi.+
23 “Ndiyeno iye anandiuza kuti, ‘Ponena za chilombo chachinayi chimenechi, pali ufumu wachinayi umene udzakhalapo padziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu ena onse. Udzadya dziko lonse lapansi ndipo udzalipondaponda ndi kuliphwanyaphwanya.+ 24 Ponena za nyanga 10 zija, mu ufumuwo mudzatuluka mafumu 10.+ Kenako mudzatulukanso mfumu ina pambuyo pa mafumu amenewa. Mfumuyo idzakhala yosiyana ndi oyambawa+ ndipo idzagonjetsa mafumu atatu.+ 25 Idzalankhula mawu otsutsana ndi Wam’mwambamwamba+ ndipo idzazunza mosalekeza oyera a Wamkulukulu.+ Idzafuna kusintha nthawi+ ndiponso lamulo+ ndipo oyerawo adzaperekedwa m’manja mwake kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi.+ 26 Bwalo la milandulo linakhala pansi,+ ndipo pamapeto pake mfumuyo anailanda ulamuliro kuti aifafanize ndi kuiwonongeratu.+
27 “‘Ufumu, ulamuliro, ndi ulemerero wa maufumu a padziko lonse lapansi zinaperekedwa kwa oyera a Wamkulukulu.+ Ufumu wawo+ udzakhalapo mpaka kalekale ndipo maulamuliro onse adzawatumikira ndi kuwamvera.’+
28 “Nkhani imeneyi yathera pamenepa. Tsopano ineyo Danieli, ndinachita mantha kwambiri moti ndinakhala ngati ndakomoka. Koma nkhaniyi ndinaisunga mumtima mwanga.”+
8 M’chaka chachitatu cha ulamuliro wa mfumu Belisazara,+ ineyo Danieli ndinaona masomphenya pambuyo pa masomphenya amene ndinaona poyambirira aja.+ 2 Nditayamba kuona masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ imene ili m’chigawo cha Elamu.+ M’masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili m’mphepete mwa mtsinje wa Ulai.+ 3 Nditakweza maso anga ndinaona nkhosa yamphongo+ itaimirira pafupi ndi mtsinjewo ndipo inali ndi nyanga ziwiri. Nyanga ziwirizi zinali zazitali koma imodzi, imene inamera pomalizira, inali yaitali kuposa inzake.+ 4 Ndinaona nkhosa yamphongoyo ikugunda kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera ndipo palibe zilombo zakutchire zimene zinaima pamaso pake komanso palibe amene anali kupulumutsa aliyense ku mphamvu zake.+ Nkhosa yamphongoyo inali kuchita zofuna zake ndipo inali kudzitama kwambiri.
5 Pamene ndinali kuganizira zimenezi, ndinangoona mbuzi yamphongo+ ikuchokera kolowera dzuwa kudutsa padziko lonse lapansi koma sinali kukhudza pansi. Pakati pa maso a mbuziyo panali nyanga yoonekera patali.+ 6 Mbuziyo inali kubwera kumene kunali nkhosa yamphongo yokhala ndi nyanga ziwiri ija, imene ndinaiona itaima pafupi ndi mtsinje, ndipo inali kubwera mwamphamvu kwa nkhosayo, ili ndi mkwiyo waukulu.
7 Mbuzi yamphongo ija ndinaiona itafika pafupi kwambiri ndi nkhosa yamphongoyo ndipo inayamba kuichitira ukali. Kenako inagunda nkhosa yamphongoyo ndi kuthyola nyanga zake ziwiri, ndipo nkhosa yamphongoyo inalibe mphamvu zotha kulimbana ndi mbuzi yamphongoyo. Choncho mbuziyo inagwetsera pansi nkhosa yamphongoyo ndi kuipondaponda ndipo inalibe woti angaipulumutse ku mphamvu za mbuziyo.+
8 Mbuzi yamphongoyo inali kudzitama mopitirira muyezo,+ koma itangokhala yamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoledwa. Pamalo pake panamera nyanga zinayi zoonekera patali zoloza kumphepo zinayi zakumwamba.+
9 Imodzi mwa nyangazi inatulutsa nyanga ina yaing’ono+ imene inayamba kukula kwambiri moloza kum’mwera, moloza kotulukira dzuwa ndiponso moloza ku Dziko Lokongola.+ 10 Inapitiriza kukula mpaka inafika kwa khamu lakumwamba,+ moti inachititsa ena mwa khamuli ndi nyenyezi zina+ kugwera padziko lapansi ndipo inazipondaponda.+ 11 Iyo inadzitama kwambiri mpaka kukafika kwa Kalonga wa khamulo.+ Inalanda Kalongayu nsembe yoyenera kuperekedwa nthawi zonse,+ ndipo malo opatulika amene iye anakhazikitsa anagwetsedwa.+ 12 Chifukwa cha uchimo,+ khamulo ndi nsembe yoyenera kuperekedwa nthawi zonse+ zinaperekedwa kwa nyangayo,+ ndipo inali kugwetsera choonadi+ pansi.+ Nyangayo inali kuchita zofuna zake ndipo inapambana.+
13 Ndiyeno ndinamva woyera winawake+ akulankhula ndipo woyera wina anafunsa woyera amene anali kulankhulayo kuti: “Kodi masomphenya okhudza nsembe yoyenera kuperekedwa nthawi zonse,+ tchimo lobweretsa chiwonongeko+ ndiponso kupondedwapondedwa kwa malo opatulika ndi kwa khamulo,+ adzakhala a nthawi yaitali bwanji?” 14 Iye anandiuza kuti: “Kufikira nsembe za tsiku ndi tsiku zokwanira 2,300, zamadzulo ndi zam’mawa, zitadutsa. Kenako malo opatulika adzakonzedwanso kuti akhale ngati mmene analili poyamba.”+
15 Ndiyeno pamene ineyo Danieli ndinali kuona masomphenyawo ndi kuyesa kuwamvetsa,+ ndinaona winawake wooneka ngati mwamuna wamphamvu ataima patsogolo panga.+ 16 Kenako ndinamva mawu a munthu wochokera kufumbi ali pakati pa mtsinje wa Ulai.+ Iye anafuula kuti: “Gabirieli,+ thandiza uyo ali apoyo kuti amvetsetse zimene waona.”+ 17 Chotero iye anabwera pafupi ndi pamene ine ndinaima. Atafika, ndinachita mantha ndipo ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi. Ndiyeno anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu,+ dziwa+ kuti masomphenyawa ndi okhudza nthawi ya mapeto.”+ 18 Pamene anali kulankhula nane ndinagona pansi chafufumimba n’kugona tulo tofa nato.+ Ndiyeno iye anandigwira ndi kundiimiritsa pamalo pomwe ndinaima paja.+ 19 Kenako anandiuza kuti: “Ine ndikudziwitsa zimene zidzachitike kumapeto kwa nthawi yopereka chiweruzo, chifukwa chakuti masomphenyawo adzakwaniritsidwa pa nthawi yoikidwiratu ya mapeto.+
20 “Nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri imene unaona, ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya.+ 21 Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi,+ ndipo nyanga yaikulu imene inali pakati pa maso ake ikuimira mfumu yoyamba.+ 22 Popeza nyangayi inathyoka ndipo panamera zina zinayi,+ pali maufumu anayi amene adzauke mu mtundu wake, koma sadzakhala ndi mphamvu ngati zake.
23 “Ku mapeto kwa ufumu wawo, uchimo wawo ukadzafika pachimake, padzauka mfumu ya maonekedwe oopsa ndiponso yomvetsa zinthu zovuta kumva.+ 24 Mfumuyo idzakula mphamvu koma osati mwa iyo yokha.+ Idzawononga zinthu zambiri+ ndipo chilichonse chimene izidzachita chidzaiyendera bwino. Idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera.+ 25 Chifukwa cha kuzindikira kwake idzathadi kugwiritsa ntchito chinyengo.+ Idzadzitukumula kwambiri mumtima mwake,+ ndipo idzawononga anthu ambiri pa nthawi imene zinthu zikuiyendera bwino.+ Mfumuyo idzalimbana ndi Kalonga wa akalonga,+ ndipo idzathyoledwa koma osati ndi dzanja la munthu.+
26 “Zinthu zimene waziona ndiponso zimene zanenedwa zokhudza madzulo ndi m’mawa, n’zoona.+ Koma iweyo usunge chinsinsi cha masomphenyawo, chifukwa ndi okhudza masiku am’tsogolo.”+
27 Ndiyeno ineyo Danieli ndinatopa kwambiri ndipo ndinadwala kwa masiku angapo.+ Kenako ndinadzuka ndi kugwira ntchito yotumikira mfumu.+ Koma ndinali wodabwa kwambiri ndi zimene ndinaona, ndipo palibe amene anazimvetsa.+
9 M’chaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero,+ wa mtundu wa Amedi,+ amene anaikidwa kukhala mfumu ya ufumu wa Akasidi,+ 2 m’chaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka za kuwonongedwa kwa Yerusalemu+ kuti zidzakhala zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi mwa kuwerenga mawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya+ olembedwa m’mabuku. 3 Ndinayang’ana+ kwa Yehova Mulungu woona kuti ndimufunefune mwa kupemphera,+ kumuchonderera, kusala kudya, kuvala ziguduli* ndi kudzithira phulusa.+ 4 Pamenepo ndinayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza machimo athu kuti:+
“Inu Yehova Mulungu woona, Mulungu wamkulu+ ndi wochititsa mantha. Anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu+ mumawasungira pangano+ ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha.+ 5 Ife tachimwa,+ talakwa, tachita zinthu zoipa ndipo takupandukirani.+ Tapatuka ndiponso tasiya malamulo anu ndi zigamulo zanu.+ 6 Sitinamvere atumiki anu aneneri,+ amene analankhula m’dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m’dziko lathu.+ 7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ife manyazi aphimba nkhope zathu lero.+ Manyazi aphimba nkhope za amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kumayiko onse akutali kumene munawabalalitsira chifukwa cha zinthu zosakhulupirika zimene anakuchitirani.+
8 “Inu Yehova, manyazi aphimba nkhope zathu, za mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu chifukwa takuchimwirani.+ 9 Inu Yehova Mulungu wathu, ndinu wachifundo+ ndi wokhululuka,+ koma ife takupandukirani.+ 10 Sitinamvere mawu anu, inu Yehova Mulungu wathu, mwa kuyenda motsatira malamulo anu amene munatiikira kudzera mwa atumiki anu, aneneri.+ 11 Anthu onse a mu Isiraeli aphwanya malamulo anu ndipo apatuka mwa kusamvera mawu anu.+ Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro+ amene analembedwa m’chilamulo cha Mose, mtumiki wa Mulungu woona, pakuti takuchimwirani. 12 Inu munachitadi zimene munachenjeza kuti mudzatichitira,+ ifeyo ndi atsogoleri athu.+ Munatigwetsera tsoka lalikulu ndipo tsoka limene lagwera Yerusalemu silinachitikeponso padziko lonse lapansi.+ 13 Masoka onse amene analembedwa m’chilamulo cha Mose+ atigwera,+ ndipo ife sitinakhazike pansi mtima wanu, inu Yehova Mulungu wathu, mwa kusiya zolakwa zathu+ ndi kusonyeza kuti tikumvetsa kuti ndinu wokhulupirika.+
14 “Inu Yehova, munakhala tcheru kuti mutigwetsere tsoka ndipo pamapeto pake munatigwetseradi tsokalo,+ pakuti inu Yehova Mulungu wathu ndinu wolungama pa ntchito zanu zonse zimene mwachita, koma ife sitinamvere mawu anu.+
15 “Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m’dziko la Iguputo ndi dzanja lamphamvu,+ amenenso munadzipangira dzina kufikira lero,+ ife tachimwa,+ tachita zinthu zoipa. 16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera.+ Pakuti chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu,+ Yerusalemu ndi anthu anu takhala chinthu chotonzedwa ndi anthu onse otizungulira.+ 17 Tsopano inu Mulungu wathu, imvani pemphero la mtumiki wanu ndi kuchonderera kwake. Malo anu opatulika amene awonongedwa+ akomereni mtima,+ inu Yehova, chifukwa cha dzina lanu. 18 Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve.+ Tsegulani maso anu kuti muone kuwonongeka kwathu ndi kwa mzinda wotchedwa ndi dzina lanu.+ Ifeyo tikukuchondererani, osati chifukwa cha zochita zathu zolungama,+ koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 19 Imvani, inu Yehova.+ Tikhululukireni, inu Yehova.+ Timvereni ndipo muchitepo kanthu,+ inu Yehova. Inu Mulungu wanga, chifukwa cha dzina lanu musazengereze,+ pakuti mzinda wanu ndi anthu anu amatchedwa ndi dzina lanu.”+
20 Pamene ndinali kulankhula, kupemphera ndi kuvomereza machimo anga+ ndi machimo a anthu a mtundu wanga Aisiraeli,+ ndiponso pamene ndinali kupempha pamaso pa Yehova Mulungu wanga kuti andikomere mtima komanso kuti akomere mtima phiri loyera la Mulungu wanga,+ 21 inde, pamene ndinali kulankhula zimenezi m’pemphero, munthu uja Gabirieli,+ amene ndinamuona m’masomphenya nditatopa kwambiri poyamba paja,+ ndinamuona akubwera kwa ine pa nthawi yopereka nsembe yamadzulo, yoperekedwa ngati mphatso.+ 22 Iye anandithandiza kuti ndimvetse pondiuza kuti:
“Iwe Danieli, tsopano ndabwera kuti ndikuthandize kumvetsa zinthu zonsezi.+ 23 Pamene unali kuyamba kupemphera ndinalandira uthenga, choncho ndabwera kudzakufotokozera za uthengawo chifukwa iwe ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.+ Tsopano khala tcheru,+ ndipo umvetsetse zinthu zimene ukuona.
24 “Pali milungu 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako+ ndi mzinda wanu woyera,+ ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo,+ athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo+ pa masomphenya ndi maulosi, ndiponso kuti adzoze Malo Opatulikitsa.+ 25 Choncho iwe uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene mawu adzamveka+ onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso,+ kufika pamene Mesiya+ Mtsogoleri+ adzaonekere, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.+ Yerusalemu adzakonzedwa ndi kumangidwanso, ndipo adzakhala ndi bwalo ndi ngalande yachitetezo. Zimenezi zidzachitika mu nthawi zovuta.
26 “Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+
“Gulu lankhondo la mtsogoleri amene akubwera lidzawononga+ mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyera amenewo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira, ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mulungu wagamula kuti padzakhale chiwonongeko.+
27 “Mesiyayo* adzasungira anthu ambiri pangano+ kwa mlungu umodzi,+ kenako pakatikati pa mlunguwo adzathetsa nsembe zanyama ndi nsembe zina zoperekedwa ngati mphatso.+
“Wowonongayo+ adzabwera pamapiko a zinthu zonyansa, ndipo zimene Mulungu wagamula zidzakhuthulidwanso pa chowonongedwacho+ kufikira chitafafanizidwa.”
10 M’chaka chachitatu cha ulamuliro wa Koresi+ mfumu ya Perisiya, panali nkhani imene Danieli anauzidwa. Danieli ameneyu anali kutchedwa Belitesazara.+ Nkhani imene anauzidwayo inali yoona ndipo inali yokhudza nkhondo yaikulu.+ Danieli anamvetsa nkhani imeneyi ndiponso zinthu zimene anaona.+
2 Masiku amenewo, ineyo Danieli, ndinali kulira+ kwa milungu itatu yathunthu. 3 Sindinadye chakudya chokoma, sindinadye nyama kapena kumwa vinyo ndipo sindinadzole mafuta kufikira milungu itatu yonseyo itatha.+ 4 Ndipo pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, pamene ndinali m’mbali mwa mtsinje waukulu, mtsinje wa Hidekeli,+ 5 ndinakweza maso anga ndipo ndinaona munthu atavala nsalu,+ atamanganso mchiuno mwake+ ndi lamba wa golide wabwino wa ku Ufazi.+ 6 Thupi lake linali ngati mwala wa kulusolito,+ nkhope yake inali yowala ngati mphezi,+ maso ake anali kuoneka ngati miyuni yamoto,+ manja ake ndi mapazi ake zinali kuoneka ngati mkuwa wonyezimira,+ ndipo mawu ake anali kumveka ngati khamu la anthu. 7 Ineyo Danieli, ndinaona ndekha munthuyo koma amuna amene ndinali nawo sanamuone.+ M’malomwake iwo anayamba kunjenjemera kwambiri moti anathawa n’kukabisala.
8 Choncho ndinatsala ndekha ndipo ndinaona masomphenya odabwitsawa. Pamenepo mphamvu zonse zinandithera, ndipo maonekedwe olemekezeka a nkhope yanga anasintha kwambiri n’kukhala omvetsa chisoni, moti ndinalibenso mphamvu.+ 9 Ndiyeno ndinayamba kumva mawu ake. Pamene ndinali kumva mawuwo ndinagona pansi+ chafufumimba n’kugona tulo tofa nato.+ 10 Pamenepo ndinamva dzanja la munthu likundikhudza,+ ndipo linayamba kundigwedeza pang’onopang’ono n’kundidzutsa. Nditadzuka ndinagwada ndi kugwira pansi ndi manja anga. 11 Iye anandiuza kuti:
“Iwe Danieli, munthu wokondedwa kwambiri,+ mvetsetsa zinthu zimene ndikukuuza+ ndipo uimirire chifukwa ndatumidwa kwa iwe.”
Atandiuza zimenezi ndinaimiriradi koma ndikunjenjemera.
12 Pamenepo iye anandiuza kuti: “Iwe Danieli, usaope,+ pakuti kuyambira tsiku loyamba pamene unatsegula mtima wako kuti umvetse tanthauzo la zinthu zimenezi,+ ndiponso pamene unadzichepetsa pamaso pa Mulungu wako,+ mawu ako akhala akumveka ndipo ine ndabwera chifukwa cha mawu akowo.+ 13 Koma kalonga+ wa ufumu wa Perisiya+ ananditsekereza+ kwa masiku 21, ndipo Mikayeli,+ mmodzi mwa akalonga aakulu+ anabwera kudzandithandiza, ndipo pa nthawi imeneyo ndinakhalabe pafupi ndi mafumu a Perisiya.+ 14 Tsopano ndabwera kudzakuthandiza kuzindikira zimene zidzagwera anthu a mtundu wako+ m’masiku otsiriza,+ chifukwa masomphenyawa+ ndi okhudza masiku am’tsogolo.”+
15 Pamene anali kulankhula nane mawu amenewa, ine ndinali nditagona chafufumimba,+ osatha kulankhula kalikonse. 16 Ndiyeno winawake wamaonekedwe ofanana ndi ana a anthu anakhudza milomo yanga.+ Atatero, ndinayamba kulankhula,+ ndipo ndinauza amene anali ataimirira patsogolo panga uja kuti: “Mbuyanga,+ ine ndinayamba kunjenjemera chifukwa cha zimene ndaona ndipo mphamvu zandithera.+ 17 Choncho ine mtumiki wanu ndingathe bwanji kulankhula nanu mbuyanga?+ Mpaka pano ndilibe mphamvu, ndipo sindikuthanso kupuma.”+
18 Ndiyeno wamaonekedwe ofanana ndi munthu wochokera kufumbi uja anandikhudza ndi kundilimbikitsa.+ 19 Iye anandiuza kuti: “Iwe munthu wokondedwa kwambiri,+ usachite mantha.+ Mtendere ukhale nawe.+ Limba mtima, ndithu, limba mtima.”+ Atangolankhula nane, ndinadzilimbitsa ndipo pamapeto pake ndinati: “Lankhulani mbuyanga+ chifukwa inu mwandilimbikitsa.”+ 20 Choncho iye anandiuza kuti:
“Kodi ukudziwadi kuti n’chifukwa chiyani ndabwera kwa iwe? Tsopano ndibwerera kuti ndikamenyane ndi kalonga wa Perisiya.+ Pamene ndikupita, nayenso kalonga wa Girisi akubwera.+ 21 Koma ndikuuza zinthu zolembedwa m’buku la choonadi,+ ndipo palibe amene akundithandiza kwambiri pa zinthu zimenezi kupatulapo Mikayeli,+ kalonga wa anthu inu.+
11 “M’chaka choyamba cha Dariyo Mmedi,+ ine ndinakhala womulimbikitsa ndipo ndinali ngati mpanda wolimba kwambiri kwa iye. 2 Tsopano ndikufotokozera choonadi:+
“Mu ufumu wa Perisiya+ mudzauka mafumu atatu, ndipo mfumu yachinayi+ idzasonkhanitsa chuma chambiri kuposa ena onsewa.+ Ndipo ikadzangokhala yamphamvu chifukwa cha chuma chakecho idzaukira ufumu wa Girisi ndi mphamvu zake zonse.+
3 “Ndiyeno mfumu yamphamvu idzauka ndi kulamulira ndi mphamvu zazikulu,+ ndipo idzachitadi zofuna zake.+ 4 Mfumuyo ikadzauka,+ ufumu wake udzasweka ndipo udzagawanika ndi kutengedwa ndi mphepo zinayi+ zakumwamba,+ koma sudzapita kwa mbadwa zake+ ndipo maufumuwo sadzafanana ndi ufumu wake. Zimenezi zidzachitika chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena.
5 “Mfumu ya kum’mwera, imene ndi mmodzi mwa akalonga ake, idzakhala yamphamvu. Koma iye* adzamugonjetsa ndipo adzalamuliradi ndi mphamvu zazikulu kuposa za ameneyo.*
6 “Ndiyeno patatha zaka zingapo iwo adzagwirizana, ndipo mwana wamkazi wa mfumu ya kum’mwera adzapita kwa mfumu ya kumpoto kuti apange mgwirizano. Koma mwana wamkaziyo sadzakhala ndi mphamvu m’dzanja lake,+ ndipo mfumuyo sidzalimba, ngakhalenso dzanja lake silidzalimba. Mwana wamkaziyo adzaperekedwa m’manja mwa anthu ena, pamodzi ndi amene anamubweretsa, amene anamubereka ndiponso amene anamuchititsa kukhala wamphamvu masiku amenewo. 7 Kenako, mphukira yochokera kumizu+ yake idzauka ndi kulowa m’malo mwake* ndipo idzafika kwa gulu lankhondo ndi kuukira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri wa mfumu ya kumpoto, moti mphukirayo idzawathira nkhondo ndi kupambana. 8 Pamenepo, mphukirayo idzapita ku Iguputo ndi milungu yawo,+ zifaniziro zawo zopangidwa ndi chitsulo chosungunula, zinthu zawo zosiririka zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi anthu amene idzawagwire. Kenako idzaima patali ndi mfumu ya kumpoto kwa zaka zingapo.
9 “Iye* adzalowa mu ufumu wa mfumu ya kum’mwera, kenako adzabwerera kudziko lakwawo.
10 “Ana ake adzadzikonzekeretsa ndi kusonkhanitsa pamodzi gulu lankhondo lalikulu. Ndiyeno mmodzi wa iwo adzafika mwamphamvu ndi kudutsa ngati madzi osefukira m’dzikolo. Koma adzabwerera, ndipo adzachita nkhondo mpaka kumzinda wake wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.
11 “Ndiyeno mfumu ya kum’mwera idzawawidwa mtima ndipo idzapita kukamenyana ndi mfumu ya kumpoto. Mfumu ya kumpoto imeneyi idzakhala ndi khamu lalikulu, koma khamulo lidzaperekedwa m’manja mwa mfumu inayo.+ 12 Khamulo lidzatengedwa, ndipo iye* adzadzitukumula mumtima mwake+ moti adzapha anthu masauzande makumimakumi. Adzakhala wamphamvu koma sadzagwiritsa ntchito mphamvu zakezo.
13 “Pamenepo mfumu ya kumpoto idzabwerera kwawo ndi kusonkhanitsa khamu lalikulu kwambiri kuposa loyamba lija, ndipo patapita nthawi, pambuyo pa zaka zingapo, idzabwera ili ndi gulu lankhondo lalikulu+ lokhala ndi katundu wambiri.+ 14 Pa nthawi imeneyo padzakhala anthu ambiri oukira mfumu ya kum’mwera.
“Ndiyeno anthu achiwawa pakati pa anthu a mtundu wako adzatengeka ndi zochitika zimenezi ndipo adzayesa kukwaniritsa masomphenya,+ koma adzapunthwa.+
15 “Kenako mfumu ya kumpoto idzabwera ndipo idzamanga chiunda chomenyerapo nkhondo*+ ndi kulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Zida zankhondo* zakum’mwera sizidzatha kulimbana nayo. Asilikali ake apamwamba kwambiri nawonso sadzatha kulimbana nayo. Iwo sadzakhala ndi mphamvu zoti apitirizebe kulimbana nayo. 16 Mfumu yobwera kudzamenyana nayo* idzachita zofuna zake, ndipo palibe adzaime pamaso pake. Mfumuyo idzaimirira m’Dziko Lokongola,+ ndipo idzapha anthu ambiri.+ 17 Iyo idzafika motsimikiza mtima+ kwambiri pamodzi ndi gulu lankhondo lamphamvu la ufumu wake. Adzachita nayo mgwirizano+ ndipo idzakwaniritsa zolinga zake.+ Iyo idzaloledwa kuti iwononge mwana wamkaziyo. Mwana wamkaziyo sadzapirira ndipo sadzapitiriza kukhala wokhulupirika kwa iyo.+ 18 Chotero iyo idzatembenukira kumadera a m’mbali mwa nyanja+ ndipo idzalanda madera ambiri. Pamenepo mtsogoleri wa asilikali adzathetsa kunyoza kwake, moti iye sadzanyozedwanso. Mtsogoleriyu adzachititsa kuti kunyozako kubwerere kwa iyo. 19 Iyo* idzabwerera kumizinda yakwawo yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Kumeneko idzapunthwa ndi kugwa ndipo sidzapezekanso.+
20 “Pamalo pake padzauka wina+ amene adzachititsa wokhometsa msonkho*+ kuyendayenda mu ufumu waulemererowo, ndipo m’masiku ochepa adzathyoka, koma osati ndi dzanja la munthu kapena pa nkhondo.
21 “Ndiyeno pamalo pa ameneyo padzauka wina wonyozeka,+ ndipo sadzamupatsa ulemerero waufumu. Iye adzabwera pa nthawi imene zinthu zikuyenda bwino+ ndipo adzatenga ufumuwo mwachinyengo.+ 22 Iye adzagonjetsa magulu ankhondo+ okhala ngati madzi osefukira, ndipo magulu ankhondowo adzawonongedwa.+ Mtsogoleri+ wa pangano+ nayenso+ adzawonongedwa. 23 Chifukwa choti iwo adzagwirizana naye, iye adzachita zinthu mwachinyengo ndi kuwaukira pogwiritsa ntchito mtundu waung’ono.+ 24 Pa nthawi imene zinthu zikuyenda bwino,+ iye adzalowa m’dera labwino kwambiri la chigawo ndipo adzachita zinthu zimene ngakhale makolo ake ndi makolo a makolo ake sanachitepo. Adzamwaza pakati pa anthu zinthu zowonongedwa, zofunkhidwa, ndi katundu wosiyanasiyana. Adzakonzera ziwembu+ malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri, koma kwa kanthawi kochepa.
25 “Iye adzasonkhanitsa mphamvu zake ndi kulimbitsa mtima wake kuti aukire mfumu ya kum’mwera ali ndi gulu lankhondo lalikulu. Mfumu ya kum’mwera nayonso idzakonzekera nkhondo mwa kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu. Koma iye* sadzalimba chifukwa adzamukonzera chiwembu. 26 Anthu amene amadya zakudya zake zokoma ndi amene adzachititsa kuti iye athyoke.
“Pamenepo gulu lake lankhondo lidzagonja ngati kuti latengedwa ndi madzi osefukira, ndipo anthu ambiri adzaphedwa.
27 “Mafumu awiri amenewa adzakhala ndi mtima wofuna kuchita zoipa, ndipo azidzalankhula bodza+ patebulo limodzi.+ Koma zolinga zawo zonse sizidzatheka+ chifukwa nthawi yamapeto sinakwane.+
28 “Choncho iye* adzabwerera kudziko lakwawo ali ndi katundu wochuluka ndipo adzakhala ndi mtima wofuna kuukira pangano lopatulika+ moti adzakwaniritsa+ zolinga zake n’kubwerera kwawo.
29 “Pa nthawi yake+ adzabwerera kwawo ndipo adzaukira dziko lakum’mwera.+ Koma sizidzakhala ngati mmene zinalili poyamba. 30 Choncho zombo za ku Kitimu+ zidzabwera ndi kumuukira ndipo adzakhala wachisoni.
“Iye adzabwerera ndi kulankhula mawu amphamvu odzudzula+ pangano lopatulika+ ndipo adzachita zofuna zake. Pamenepo iye adzabwerera ndi kuganizira anthu osiya pangano lopatulika. 31 Ndiyeno padzauka magulu ankhondo* otuluka mwa iye. Maguluwo adzaipitsa malo opatulika+ amene ndi malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri, ndipo adzachotsa nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse.+
“Iwo adzaika pamalowo chinthu chonyansa+ chobweretsa chiwonongeko.+
32 “Anthu amene akuchita zinthu zoipa motsutsana ndi pangano+ adzawatsogolera ku mpatuko+ pogwiritsa ntchito mawu achinyengo.+ Koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo+ adzapambana+ ndi kukwaniritsa zolinga zawo. 33 Anthu ozindikira+ pakati pa anthuwo adzathandiza anthu ambiri kumvetsa zinthu.+ Iwo adzapunthwa kwa kanthawi ndi lupanga ndi malawi a moto. Adzapunthwanso mwa kutengedwa ukapolo ndi kuwonongedwa kwa zinthu zawo.+ 34 Koma akadzapunthwa adzathandizidwa ndi thandizo lochepa,+ ndipo ambiri adzadziphatika kwa iwo mwachinyengo.+ 35 Ena mwa anthu ozindikirawo adzapunthwa.+ Zidzatero kuti ntchito yoyenga ichitike* ndiponso kuti anthu ozindikira atsukidwe ndi kuyeretsedwa+ kufikira nthawi ya mapeto,+ pakuti nthawi yake idzafika.+
36 “Mfumuyo idzachita zofuna zake ndipo idzadzikweza ndi kudzikuza kuposa mulungu aliyense.+ Iyo idzalankhula zinthu zodabwitsa zotsutsana ndi Mulungu wa milungu.+ Idzapambana kufikira chidzudzulo champhamvu chitaperekedwa chonse,+ chifukwa chinthu chimene chakonzedwa chiyenera kuchitika. 37 Iyo sidzaganizira Mulungu wa makolo ake. Sidzaganiziranso zofuna za akazi kapena za mulungu wina aliyense koma idzadzikweza pamwamba pa aliyense.+ 38 Ndipo idzapereka ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Idzapereka ulemu kwa mulungu amene makolo ake sanamudziwe ndipo idzapatsa mulunguyo golide, siliva, miyala yamtengo wapatali ndi zinthu zosiririka. 39 Mfumuyo idzakwaniritsa zolinga zake polimbana ndi malo otetezeka kwambiri okhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo idzachita zimenezi pamodzi ndi mulungu wachilendo. Aliyense woivomereza idzamupatsa ulemerero waukulu ndipo idzachititsa anthu oterowo kulamulira pakati pa anthu ambiri. Iyo idzagawa malo ndi kuwagulitsa.
40 “Ndiyeno m’nthawi ya mapeto mfumu ya kum’mwera+ idzayamba kukankhana nayo ndipo mfumu ya kumpoto idzabwera mwamphamvu kudzamenyana nayo. Idzabwera ndi magaleta, asilikali okwera pamahatchi* ndi zombo zambiri. Mfumuyo idzalowa m’mayiko ndi kudutsamo ngati madzi osefukira. 41 Iyo idzalowanso+ m’Dziko Lokongola+ ndipo idzachititsa mayiko ambiri kupunthwa,+ koma Edomu, Mowabu+ ndi mbali yaikulu ya ana a Amoni adzapulumuka m’manja mwake. 42 Iyo idzapitirizabe kutambasulira dzanja lake pa mayiko ndipo dziko la Iguputo+ silidzapulumuka. 43 Idzalamulira chuma chobisika cha golide ndi siliva. Ndipo idzalamuliranso zinthu zonse zosiririka za dziko la Iguputo. Anthu a ku Libiya ndi a ku Itiyopiya adzakhala akumutsatira.
44 “Koma kotulukira dzuwa+ ndi kumpoto kudzachokera mauthenga amene adzaisokoneza.+ Pamenepo iyo idzapita ndi ukali waukulu kuti ikafafanize ndi kuwononga ambiri.+ 45 Ndipo idzamanga mahema okhala ngati nyumba yachifumu pakati pa nyanja yaikulu ndi phiri lopatulika la Dziko Lokongola.+ Ndiyeno iyo idzafika kumapeto a moyo wake+ ndipo sipadzapezeka woithandiza.+
12 “Pa nthawi imeneyo Mikayeli,+ kalonga wamkulu+ amene waimirira+ kuti athandize anthu a mtundu wako, adzaimirira.+ Ndiyeno padzafika nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kufikira nthawi imeneyo.+ Pa nthawi imeneyo aliyense mwa anthu a mtundu wako amene dzina lake lidzakhala litalembedwa m’buku+ adzapulumuka.+ 2 Anthu ambiri amene agona munthaka adzauka.+ Ena adzalandira moyo wosatha+ koma ena adzalandira chitonzo ndipo adzadedwa mpaka kalekale.+
3 “Anthu ozindikira adzawala ngati kuwala kwa kuthambo.+ Ndipo amene akuthandiza anthu ambiri kukhala olungama+ adzawala ngati nyenyezi mpaka kalekale, inde, kwamuyaya.
4 “Koma iwe Danieli, sunga mawuwa mwachinsinsi ndipo utseke ndi kumata bukuli+ kufikira nthawi yamapeto.+ Anthu ambiri adzayenda uku ndi uku ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona.”+
5 Ndiyeno ineyo Danieli nditayang’ana, ndinangoona angelo ena awiri ataimirira.+ Mngelo wina anaimirira m’mbali mwa mtsinje tsidya lino, ndipo wina anaimirira tsidya linalo.+ 6 Kenako mmodzi mwa angelowo anafunsa munthu wovala nsalu uja,+ amene anaimirira pamwamba pa madzi a mumtsinjewo, kuti: “Kodi zidzatenga nthawi yaitali bwanji kuti zinthu zodabwitsazi zikwaniritsidwe zonse?”+ 7 Pamenepo ndinamva mwamuna wovala nsalu uja, amene anaimirira pamwamba pa madzi a mumtsinje akuyankha. Poyankhapo, anakweza m’mwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere ndi kulumbira+ pa Iye amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzapita nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu, ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.+ Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya+ mphamvu za anthu oyera, zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”
8 Tsopano ine ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziwe tanthauzo lake.+ Choncho ndinafunsa kuti: “Inu mbuyanga, kodi zinthu zimenezi zidzatha bwanji?”+
9 Iye anandiyankha kuti: “Pita Danieli, pakuti mawuwa asungidwa mwachinsinsi ndipo atsekedwa ndi kumatidwa kufikira nthawi yamapeto.+ 10 Anthu ambiri adzadzitsuka,+ adzadziyeretsa+ ndipo adzayengedwa.+ Anthu oipa adzachita zinthu zoipa+ ndipo palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa,+ koma anthu ozindikira adzawamvetsetsa.+
11 “Kuchokera pa nthawi imene nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse+ zidzachotsedwa,+ ndiponso pamene chinthu chonyansa+ chobweretsa chiwonongeko chidzaikidwa, padzapita masiku 1,290.
12 “Wodala+ ndi munthu amene akuyembekezera mpaka kufika ku mapeto a masiku 1,335.
13 “Ndiyeno iwe pita ku mapeto+ ndipo udzapuma.+ Koma udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.”+
Kapena kuti “zolemba.”
“Akasidi” amenewa anali kagulu kapadera ka anthu amene anali kudziona kuti anali ndi luso lolosera zam’tsogolo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
“Mkulu wa boma” ameneyu anali pansi pa Masatarapi m’boma la Babulo.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.
Onani mawu a m’munsi pa Da 2:48.
Onani mawu a m’munsi pa Da 2:2.
Onani mawu a m’munsi pa Da 2:2.
Mawu ake enieni, “zamoyo zoyera.”
Kapena kuti “patsindwi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Onani mawu a m’munsi pa Da 2:2.
Anthu olemera, olemekezeka ndi mafumu ndi amene ankavala zovala zamtundu umenewu.
Mawu achiaramu akuti “PERESI” ndi otchulira chinthu chimodzi. Zikakhala zinthu zambiri mawu ake ndi “PARASINI” amene ali muvesi 25.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.
Ena amati “nyalugwe.”
Ena amati “masaka.”
Mawu ake enieni, “Iye.”
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “magulu ankhondo.”
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kum’mwera.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Mawu amene tawamasulira kuti “wokhometsa msonkho” akhozanso kutanthauza munthu amene amalemba anthu ntchito yausilikali.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.
Mawu ake enieni, “zida zankhondo.”
Mawu ake enieni, “kuti ntchito yoyenga ichitike chifukwa cha iwo.”
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”