Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Joel 1:1-3:21
  • Yoweli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yoweli
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Yoweli

Yoweli

1 Yehova analankhula+ kudzera mwa Yoweli mwana wa Petueli kuti:

2 “Tamverani inu akulu ndipo mutchere khutu inu nonse okhala m’dzikoli.+ Kodi zinthu izi zinachitikapo m’masiku anu, kapena m’masiku a makolo anu?+ 3 Fotokozerani ana anu za zinthu zimenezi. Ana anu adzafotokozere ana awo, ndipo ana a ana anuwo adzafotokozerenso m’badwo wotsatira.+ 4 Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe.+ Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+

5 “Galamukani zidakwa inu.+ Lirani ndipo fuulani+ chifukwa cha vinyo wotsekemera*+ inu nonse okonda kumwa vinyo, pakuti vinyoyo wachotsedwa pakamwa panu.+ 6 Pali mtundu umene walowa m’dziko langa. Mtunduwo ndi wamphamvu ndipo anthu ake ndi osawerengeka.+ Mano ndiponso nsagwadwa zawo zili ngati za mikango.+ 7 Iwo achititsa mtengo wanga wa mpesa kukhala chinthu chodabwitsa+ ndipo mtengo wanga wa mkuyu ausandutsa chitsa.+ Nthambi za mitengo imeneyi azichotsa makungwa n’kuzitayira kutali.+ Mphukira zake azichotsa makungwa ndipo zauma. 8 Lirani momvetsa chisoni ngati mmene amalirira namwali amene wavala chiguduli*+ polirira mwamuna amene anali kufuna kumukwatira.

9 “Nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa+ zachotsedwa m’nyumba ya Yehova. Ansembe, atumiki+ a Yehova, alira.+ 10 Munda wawonongedwa+ ndipo nthaka ikulira+ pakuti mbewu zawonongedwa. Vinyo watsopano wauma+ ndipo mafuta atha.+ 11 Alimi achita manyazi+ chifukwa cha tirigu ndi barele ndipo osamalira minda ya mpesa akulira mofuula. Zili choncho chifukwa chakuti zokolola za m’munda zawonongeka.+ 12 Kukondwera kwachoka pamaso pa ana a anthu.+ Ndithu mtengo wa mpesa wauma ndiponso mtengo wa mkuyu wafota. Mtengo wa makangaza* komanso mtengo wa kanjedza, mtengo wa maapozi ndi mitengo yonse yakuthengo yauma.+

13 “Dzimangirireni m’chiuno ndipo dzigugudeni pachifuwa,+ inu ansembe. Lirani mofuula, inu atumiki a paguwa lansembe.+ Lowani, valani ziguduli usiku wonse inu atumiki a Mulungu wanga, pakuti nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa zachotsedwa m’nyumba ya Mulungu wanu.+ 14 Konzekerani nthawi yosala kudya.+ Itanitsani msonkhano wapadera.+ Sonkhanitsani pamodzi akulu ndi anthu onse okhala m’dzikoli kuti akumane kunyumba ya Yehova Mulungu wanu+ ndipo alirire Yehova kuti awathandize.+

15 “Kalanga ine! Tsiku lija likufika.+ Tsiku la Yehova lili pafupi.+ Tsikulo lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse. 16 Kodi chakudya sanatichotsere pamaso pathu? Kodi kukondwera ndi kusangalala sizinachotsedwe m’nyumba ya Mulungu wathu?+ 17 Nkhuyu zouma zawonongeka mafosholo ali pamwamba pake. Nkhokwe zawonongedwa. Nyumba zosungiramo zinthu zapasulidwa, pakuti mbewu zatha. 18 Ziweto zausa moyo. Gulu la ng’ombe likuyendayenda mosokonezeka pakuti kulibe msipu woti zidye.+ Ndiponso gulu la nkhosa ndi limene lalangidwa chifukwa cha uchimo.

19 “Ine ndidzaitana inu Yehova,+ pakuti moto wawononga malo odyetserako ziweto m’chipululu ndipo moto walawilawi wanyeketsa mitengo yonse yakuthengo.+ 20 Chifukwa chakuti mitsinje ya madzi yauma,+ ndipo moto wawononga malo odyetserako ziweto m’chipululu, zilombo zakutchire nazonso zikukufunani kwambiri.”+

2 “Lizani lipenga m’Ziyoni+ amuna inu ndipo fuulani mfuu yankhondo+ m’phiri langa loyera.+ Anthu onse okhala m’dzikoli anjenjemere,+ pakuti tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi! 2 Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+ tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani. Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa m’bandakucha kumakhalira pamwamba pa mapiri.+

“Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+ Palibe mtundu wina umene ungafanane nawo kuyambira nthawi yakale+ ndipo sipadzakhalanso wina wofanana nawo ku mibadwomibadwo. 3 Patsogolo pawo moto wawononga+ ndipo kumbuyo kwawo moto walawilawi ukunyeketsa.+ Patsogolo pawo pali dziko ngati la Edeni+ koma kumbuyo kwawo kuli chipululu chowonongeka ndipo palibe chilichonse chopulumuka.

4 “Mtundu wa anthuwo umaoneka ngati mahatchi,* ndipo amathamanga ngati mahatchi amphamvu.+ 5 Amadumphadumpha ndipo amachita mkokomo ngati magaleta oyenda pamwamba pa mapiri+ ndiponso ngati moto walawilawi umene ukutentha mapesi.+ Iwo ali ngati anthu amphamvu amene afola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+ 6 Mitundu ya anthu idzamva ululu waukulu+ chifukwa cha mtunduwo, ndipo nkhope zawo zonse zidzakhala zankhawa.+

7 “Amathamanga ngati amuna amphamvu.+ Amakwera khoma ngati amuna ankhondo. Aliyense amayenda m’njira yake ndipo saphonya njira zawo.+ 8 Iwo sakankhanakankhana ndipo amayendabe ngati mwamuna wamphamvu amene akuyenda panjira yake. Wina akalasidwa ndi kugwa enawo sabwerera m’mbuyo.

9 “Iwo amathamangira m’mizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda. Amakwera nyumba ndipo amalowa m’nyumbamo kudzera pawindo ngati mbala. 10 Dziko lanjenjemera pamaso pawo ndipo kumwamba kwagwedezeka. Dzuwa ndi mwezi zada+ ndipo nyenyezi zaleka kuwala.+ 11 Yehova adzalankhula+ pamaso pa asilikali ake ankhondo+ pakuti anthu a mumsasa wake ndi ambiri.+ Amene akukwaniritsa mawu ake ali ndi mphamvu. Tsiku la Yehova ndi lalikulu+ ndi lochititsa mantha. Ndani angaime pa tsiku limeneli?”+

12 Yehova wanenanso kuti, “Tsopano bwererani kwa ine ndi mtima wanu wonse.+ Salani kudya,+ lirani momvetsa chisoni ndiponso mokuwa.+ 13 Ng’ambani mitima yanu+ osati zovala zanu+ ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu pakuti iye ndi wachisomo, wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+ Ndithu, iye adzakumverani chisoni chifukwa cha tsokalo.+ 14 Ndani akudziwa kuti mwina adzasintha maganizo ake ndi kukumverani chisoni+ ndipo kenako adzakusiyirani madalitso,+ nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa kuti mupereke kwa Yehova Mulungu wanu?

15 “Lizani lipenga la nyanga ya nkhosa mu Ziyoni amuna inu.+ Konzekerani nthawi yosala kudya.+ Itanitsani msonkhano wapadera.+ 16 Sonkhanitsani anthu onse pamodzi ndipo muyeretse mpingo.+ Sonkhanitsani amuna achikulire. Sonkhanitsani pamodzi ana ndi makanda oyamwa.+ Mkwati atuluke m’chipinda chake ndipo mkwatibwi atuluke kumalo ake ogona.

17 “Ansembe ndi atumiki a Yehova alire m’khonde mwa guwa lansembe+ ndipo anene kuti, ‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu ndipo musachititse manyazi cholowa chanu+ kuti mitundu ya anthu iwalamulire. Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+ 18 Ndiyeno Yehova adzachitira nsanje dziko lake+ ndipo adzamvera chifundo anthu ake.+ 19 Pamenepo Yehova adzayankha ndi kuuza anthu ake kuti, ‘Tsopano ndikukutumizirani mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta. Anthu inu mudzakhutadi zinthu zimenezi.+ Ine sindidzakuchititsaninso kukhala chinthu chotonzedwa pakati pa anthu a mitundu ina.+ 20 Ndidzakuchotserani mdani wa kumpoto+ kuti akhale kutali ndi inu. Ndidzamuthamangitsira kudziko lopanda madzi ndi labwinja, nkhope yake itayang’ana kunyanja ya kum’mawa*+ ndipo nkhongo yake italoza kunyanja ya kumadzulo.*+ Fungo lake lonunkha lidzamveka ndipo fungo lake loipalo lidzapitirizabe kumveka+ pakuti Mulungu adzachita zinthu zazikulu.’

21 “Usachite mantha iwe dziko. Kondwera ndi kusangalala, pakuti Yehova adzachita zinthu zazikulu.+ 22 Inu zilombo zakutchire musachite mantha,+ pakuti malo odyetserako ziweto a m’chipululu adzamera msipu wobiriwira.+ Mitengo nayonso idzabereka zipatso.+ Mtengo wa mkuyu ndi mtengo wa mpesa udzatulutsa zipatso zake zonse.+ 23 Inu ana aamuna a Ziyoni kondwerani ndi kusangalala chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+ Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera+ ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+ 24 Malo opunthira mbewu adzadzaza ndi mbewu zopunthidwa ndipo malo ogweramo vinyo watsopano ndi mafuta adzasefukira.+ 25 Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonse zimene dzombe ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko, mphemvu ndi mbozi zinadya. Limeneli ndi gulu langa lankhondo lamphamvu limene ndinatumiza pakati panu.+ 26 Pamenepo mudzadya ndi kukhuta+ ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu+ amene wakuchitirani zodabwitsa.+ Anthu anga sadzachita manyazi mpaka kalekale.*+ 27 Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndili pakati pa Isiraeli,+ ndiponso kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu ndipo palibenso Mulungu wina.+ Anthu anga sadzachita manyazi mpaka kalekale.

28 “Zimenezi zikadzachitika ndidzatsanulira mzimu wanga+ pa chamoyo chilichonse,+ ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi+ adzanenera. Amuna achikulire adzalota maloto ndipo anyamata adzaona masomphenya. 29 Masiku amenewo ndidzatsanuliranso mzimu wanga pa antchito anu aamuna ndi aakazi.+

30 “Ndidzachita zodabwitsa kuthambo+ ndi padziko lapansi. Ndidzachititsa kuti pakhale magazi, moto ndi utsi wokwera kumwamba.+ 31 Dzuwa lidzasanduka mdima,+ ndipo mwezi udzasanduka magazi.+ Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanafike.+ 32 Ndiyeno aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka,+ pakuti m’phiri la Ziyoni ndiponso mu Yerusalemu mudzakhala anthu opulumuka+ monga mmene Yehova ananenera. Amenewa ndi anthu amene Yehova akuwaitana.”+

3 “Ndiyeno masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ ndidzabwezeretsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amene anagwidwa ukapolo.+ 2 Ine ndidzasonkhanitsanso pamodzi mitundu yonse ya anthu+ ndi kuibweretsa m’chigwa cha Yehosafati+ ndipo ndidzaiweruza chifukwa cha anthu anga ndi cholowa changa, Isiraeli.+ Mitundu imeneyi inamwaza Isiraeli pakati pa mitundu ya anthu ndiponso inagawana dziko langa.+ 3 Mitunduyi inali kuchitira maere anthu anga+ ndipo inali kupereka mwana wamwamuna kuti akhale malipiro a hule.+ Inali kupereka mwana wamkazi kuti akhale malipiro a vinyo woti amwe.

4 “Tsopano ndili nawenso chiyani iwe Turo ndi Sidoni+ ndiponso inu nonse okhala m’chigawo cha Filisitiya?+ Kodi zimenezi ndi zimene mukundipatsa monga mphoto yanga? Ngati mukundipatsa zimenezi, ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+ 5 Chifukwa chakuti anthu inu mwatenga siliva ndi golide wanga,+ mwabweretsa zinthu zanga zamtengo wapatali mu akachisi anu,+ 6 mwagulitsa ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu+ kwa ana a Agiriki,+ ndi cholinga choti muwachotse ndi kuwapititsa kutali ndi dziko lawo,+ 7 tsopano ndiwatenga kuti achoke kumalo amene munawagulitsa+ ndipo ndikubwezerani zimene munachita.+ 8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa ana a Yuda.+ Ana a Yudawo adzawagulitsa kwa amuna a ku Sheba,+ mtundu wa anthu akutali.+ Ine Yehova ndanena zimenezi.

9 “Anthu inu, lengezani pakati pa mitundu ina kuti,+ ‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu!+ Amuna onse ankhondo abwere!+ 10 Sulani makasu anu a pulawo kuti akhale malupanga, ndiponso zida zanu zosadzira mitengo+ kuti zikhale mikondo ing’onoing’ono. Munthu wofooka anene kuti: “Ndine mwamuna wamphamvu.”+ 11 Inu mitundu ya anthu yokhala mozungulira, bwerani mudzathandizane+ ndipo nonse musonkhane pamodzi.’”+

Inu Yehova, bweretsani ankhondo anu kumalo amenewo.+

12 “Mitundu ya anthu inyamuke ndi kubwera kuchigwa cha Yehosafati,+ pakuti kumeneko ndidzakhala pansi kuti ndiweruze mitundu yonse ya anthu yokhala mozungulira.+

13 “Yambani kumweta ndi chikwakwa,+ pakuti zokolola zacha.+ Bwerani, tsikirani kuno, pakuti moponderamo mphesa mwadzaza.+ Malo ogweramo vinyo wake asefukira, pakuti zoipa za anthu a mitundu ina zachuluka kwambiri.+ 14 Makamu ambirimbiri a anthu ali m’chigwa+ choweruzira mlandu, pakuti tsiku la Yehova layandikira m’chigwa choweruzira mlandu.+ 15 Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima, ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala.+ 16 Yehova adzabangula ngati mkango kuchokera m’Ziyoni ndipo adzalankhula ali ku Yerusalemu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka+ koma Yehova adzakhala chitetezo kwa anthu ake,+ ndipo adzakhala malo a chitetezo champhamvu kwa ana a Isiraeli.+ 17 Pamenepo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu,+ amene ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.+ Yerusalemu adzakhala malo anga opatulika,+ ndipo alendo sadzadutsanso mmenemo.+

18 “Nthawi imeneyo mapiri adzachucha vinyo wotsekemera.+ Mkaka udzayenda pazitunda ndipo m’mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi. Kasupe wamadzi adzatuluka m’nyumba ya Yehova+ ndi kuthirira chigwa cha Mitengo ya Mthethe.+ 19 Iguputo adzasanduka bwinja,+ Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu+ chifukwa cha chiwawa chimene anachitira ana a Yuda, ndiponso chifukwa chokhetsa magazi osalakwa m’dziko la Yudalo.+ 20 Koma mu Yuda mudzakhala anthu mpaka kalekale,+ ndipo mu Yerusalemu mudzakhala anthu ku mibadwomibadwo.+ 21 Magazi awo amene anali ndi mlandu adzakhala opanda mlandu,+ ndipo Yehova azidzakhala mu Ziyoni.”+

Ena amati “wonzuna.”

Ena amati “saka.”

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”

Kutanthauza, “Nyanja Yamchere.”

Kutanthauza, “Nyanja Yaikulu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena