Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Amos 1:1-9:15
  • Amosi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amosi
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Amosi

Amosi

1 Awa ndi mawu a Amosi amene anali mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa.+ Anauzidwa mawu amenewa m’masomphenya okhudza Isiraeli,+ m’masiku a Uziya+ mfumu ya Yuda ndi m’masiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi,+ mfumu ya Isiraeli, zaka ziwiri chivomezi chisanachitike.+ 2 Iye anati:

“Yehova adzabangula ngati mkango mu Ziyoni,+ ndipo adzafuula mu Yerusalemu.+ Malo amene abusa amadyetserako ziweto adzalira, ndipo pansonga ya phiri la Karimeli padzauma.”+

3 “Yehova wanena kuti, ‘“Popeza kuti Damasiko+ anapanduka mobwerezabwereza,* sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anapuntha Giliyadi+ ndi zida zachitsulo zopunthira. 4 Ndidzatumiza moto+ panyumba ya Hazaeli,+ ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Beni-hadadi.+ 5 Ndidzathyola mipiringidzo ya zipata za Damasiko+ ndi kupha anthu a ku Bikati-aveni. Ndidzaphanso munthu wogwira ndodo yachifumu wa ku Beti-edeni, ndipo anthu a ku Siriya adzatengedwa kupita ku ukapolo ku Kiri,”+ watero Yehova.’

6 “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti Gaza wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anthu onse ogwidwa ukapolo+ anawapereka ku Edomu.+ 7 Ndidzatumiza moto pakhoma la Gaza+ ndipo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo. 8 Ndidzapha anthu a ku Asidodi+ pamodzi ndi wogwira ndodo yachifumu wa ku Asikeloni.+ Ndidzalanga+ Ekironi+ ndipo ndidzafafaniza otsala mwa Afilisiti,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’

9 “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Turo+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo, ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pa ubale.+ 10 Ndidzatumiza moto pakhoma la Turo ndipo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo.’+

11 “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anathamangitsa m’bale wake ndi lupanga,+ sanasonyeze chifundo,+ akupitiriza kukhadzulakhadzula zinthu ali wokwiya komanso akukhalabe wokwiya mosalekeza.+ 12 Ndidzatumiza moto ku Temani+ ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za ku Bozira.’+

13 “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti ana a Amoni+ andipandukira mobwerezabwereza, sindidzawasinthira chigamulo changa.+ Sindidzawasinthira chigamulocho chifukwa chakuti anatumbula akazi apakati a ku Giliyadi ndi cholinga chakuti afutukule malo awo okhala.+ 14 Ndidzayatsa mpanda wa Raba+ ndipo motowo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo. Padzakhala chizindikiro chochenjeza pa tsiku la nkhondo ndiponso mphepo yamkuntho pa tsiku la chimvula champhamvu.+ 15 Pamenepo mfumu yawo idzagwidwa ndi kupita ku ukapolo pamodzi ndi akalonga ake,”+ watero Yehova.’

2 “Yehova wanena kuti, ‘“Popeza kuti Mowabu+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anatentha mafupa a mfumu ya Edomu kuti apeze laimu.+ 2 Ndidzatumiza moto ku Mowabu, ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Kerioti.+ Mowabu adzafa pakati pa phokoso la asilikali, kulira kwa chizindikiro chochenjeza ndiponso lipenga la nyanga ya nkhosa.+ 3 Ndidzapha woweruza pamodzi ndi akalonga ake onse amene ali naye limodzi,”+ watero Yehova.’

4 “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Yuda+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anakana lamulo la Yehova+ ndiponso sanasunge malangizo ake koma anasocheretsedwa ndi mabodza+ amene makolo awo anali kutsatira.+ 5 Ndidzatumiza moto mu Yuda ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Yerusalemu.’+

6 “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Isiraeli anapanduka mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anagulitsa munthu wolungama kuti apeze siliva komanso anagulitsa munthu wosauka pa mtengo wa nsapato.+ 7 Iwo akufunitsitsa kuti fumbi la padziko lapansi ligwere pamitu ya anthu wamba+ ndipo sakuchitira chilungamo anthu ofatsa.+ Mwana pamodzi ndi bambo ake akugona ndi mtsikana mmodzi+ ndi cholinga chofuna kuipitsa dzina langa loyera.+ 8 Iwo amayala zovala pafupi ndi guwa lililonse lansembe+ ndi kugonapo. Zovala zimenezo zimakhala zimene alanda anthu ena monga chikole.+ Amagula vinyo ndi ndalama zimene alipiritsa anthu ndipo amakamwera vinyoyo kunyumba za milungu yawo.’+

9 “‘Koma ine ndinawononga Aamori+ chifukwa cha anthu anga. Aamoriwo misinkhu yawo inali yofanana ndi mitengo ya mkungudza ndipo mphamvu zawo zinali zofanana ndi za mitengo ikuluikulu.+ Ndinawononga zipatso zawo m’mwamba ndiponso mizu yawo pansi.+ 10 Koma ine ndinatulutsa anthu inu m’dziko la Iguputo+ ndi kukuyendetsani m’chipululu zaka 40+ kuti mukatenge dziko la Aamori.+ 11 Ena mwa ana anu ndinali kuwachititsa kukhala aneneri+ ndipo ena ndinali kuwachititsa kukhala Anaziri.+ Kodi mmenemu si mmene zinayenera kukhalira, inu ana a Isiraeli?’ watero Yehova.

12 “‘Koma inu munapitiriza kupatsa Anaziri vinyo kuti amwe+ ndipo aneneri munawalamula kuti: “Musamanenere.”+ 13 Tsopano ine ndigwedeza nthaka imene mwapondapo ngati mmene ngolo imene yanyamula tirigu amene amumweta kumene imagwedezekera. 14 Malo othawirapo munthu waliwiro adzawonongeka+ ndipo palibe munthu wamphamvu amene adzalimbe, komanso palibe munthu wamphamvu amene adzapulumutse moyo wake.+ 15 Munthu wogwira uta sadzaima, munthu waliwiro kwambiri sadzatha kuthawa ndipo wokwera pahatchi* sadzatha kupulumutsa moyo wake.+ 16 Ndipo munthu wolimba mtima pakati pa anthu amphamvu adzathawa ali maliseche pa tsiku limenelo,’+ watero Yehova.”

3 “Tamverani mawu amene Yehova wanena okhudza inu+ ana Aisiraeli, mawu okhudza banja lonse limene ndinalitulutsa m’dziko la Iguputo.+ Mawuwo ndi akuti, 2 ‘Pa mabanja onse apadziko lapansi+ ine ndimadziwa inu nokha.+ Choncho ndidzakulangani chifukwa cha zolakwa zanu zonse.+

3 “‘Kodi anthu awiri amayenda pamodzi asanapangane ndi kukumana mogwirizana ndi pangano lawolo?+ 4 Kodi mkango umabangula m’nkhalango usanagwire nyama?+ Kodi mkango wamphamvu umalira m’malo ake obisalamo usanagwire kalikonse? 5 Kodi mbalame imakodwa mumsampha pansi, pamene palibe msampha?+ Kodi msampha umafwamphuka kuchokera pansi usanagwire kalikonse? 6 Lipenga la nyanga ya nkhosa likalira mumzinda, kodi anthu sanjenjemera?+ Kodi tsoka likagwa mumzinda si Yehova amene wachititsa? 7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+ 8 Mkango wabangula!+ Ndani sachita mantha? Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa walankhula! Ndani sanenera?’+

9 “‘Lengezani izi pansanja zokhalamo za ku Asidodi ndi pansanja zokhalamo za m’dziko la Iguputo.+ Munene kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti muukire mapiri a Samariya+ ndipo onani zinthu zambiri zachisokonezo ndi zachinyengo zimene zikuchitika mumzinda umenewo.+ 10 Anthuwo sadziwa kuchita zolungama,+ ndipo asonkhanitsa munsanja zawo zokhalamo zinthu zimene anafunkha mwachiwawa,”+ watero Yehova.’

11 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali mdani amene wazungulira dziko lonse+ ndipo ameneyo adzakukhalitsa wopanda mphamvu ndipo adzafunkha nsanja zako zokhalamo.’+

12 “Yehova wanena kuti, ‘Monga mmene m’busa amapulumutsira ziboda ziwiri za chiweto ndi kachidutswa ka khutu m’kamwa mwa mkango,+ nawonso ana a Isiraeli amene akukhala m’Samariya pamipando yapamwamba+ ndi kugona pamabedi a ku Damasiko+ adzapulumuka ochepa chabe m’manja mwa adani awo.’

13 “‘Tamverani ndipo muchitire umboni,+ inu a nyumba ya Yakobo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Mulungu wa makamu. 14 ‘Pa tsiku limene ndidzalanga Isiraeli+ chifukwa cha kupanduka kwake, ndidzaperekanso chiweruzo pamaguwa ansembe a ku Beteli+ ndipo nyanga za guwa lansembe zidzazulidwa ndi kugwa pansi.+ 15 Nyumba yokhalamo m’nyengo yozizira+ ndi nyumba yokhalamo m’nyengo yotentha+ ndidzazigwetsa.’

“‘Nyumba zaminyanga ya njovu zidzafafanizidwa+ ndipo nyumba zambiri zidzawonongedwa,’+ watero Yehova.”

4 “Tamverani mawu awa, inu ng’ombe zazikazi za ku Basana,+ zokhala m’phiri la Samariya,+ inu amene mukuchitira zachinyengo anthu onyozeka,+ amene mukuphwanya anthu osauka ndipo mukuuza ambuye anu kuti, ‘Tipatseni chakumwa kuti timwe!’ 2 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walumbira mwa kuyera kwake+ kuti, ‘“Taonani! Masiku adzafika pamene mudzanyamulidwa ndi ngowe zokolera nyama ndipo otsala anu adzawakola ndi mbedza za nsomba.+ 3 Aliyense wa inu adzatulukira pachibowo cha mpanda+ chimene ali nacho pafupi ndipo mudzaponyedwa kunja, ku Harimoni,” watero Yehova.’

4 “‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa.+ Muzichita zolakwa mobwerezabwereza ku Giligala+ ndipo muzibweretsa nsembe zanu m’mawa. Pa tsiku lachitatu, muzibweretsa chakhumi* chanu.+ 5 Perekani nsembe zoyamikira zautsi kuchokera pa zinthu zokhala ndi chofufumitsa+ ndipo lengezani ndi kufalitsa za nsembe zaufulu+ pakuti ndi zimene mukukonda, inu ana a Isiraeli,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

6 “‘Komanso ine ndinakupatsani njala*+ m’mizinda yanu yonse ndipo munali kusowa chakudya m’malo anu onse okhala,+ koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

7 “‘Ine ndinakumanani mvula kutatsala miyezi itatu kuti mukolole.+ Ndinagwetsa mvula pamzinda umodzi koma pamzinda wina sindinagwetsepo mvula. Mvula inagwa pamunda umodzi koma pamunda wina sindinagwetsepo mvula ndipo unauma.+ 8 Anthu a m’mizinda iwiri kapena itatu anayenda movutikira kupita kumzinda wina kuti akamwe madzi+ ndipo ludzu lawo silinathe, koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

9 “‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso ndi matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina ndipo mbozi zinawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+ komabe inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

10 “‘Anthu inu ndinakutumizirani mliri wofanana ndi umene unachitika ku Iguputo.+ Ndinapha anyamata anu ndi lupanga+ ndipo mahatchi anu analandidwa.+ Ndinachititsa fungo lonunkha lotuluka m’misasa yanu kufika kumphuno zanu,+ koma inu simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

11 “‘Ndinabweretsa chiwonongeko pakati pa anthu inu chofanana ndi chimene Mulungu anabweretsa pa Sodomu ndi Gomora.+ Pamenepo inu munakhala ngati chitsa cholanditsidwa pamoto+ koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.

12 “Tsopano zinthu zofanana ndi zimenezi ndi zimene ndidzakuchitira, iwe Isiraeli. Ndipo chifukwa chakuti ndidzakuchitira zimenezi, konzekera kukumana ndi Mulungu wako,+ iwe Isiraeli. 13 Taona! Yehova Mulungu wa makamu ndilo dzina+ la amene anapanga mapiri,+ analenga mphepo,+ amene amafotokozera munthu zimene akuganiza,+ amene amachititsa kuwala kwa m’bandakucha kukhala mdima+ ndiponso amene amaponda malo okwezeka a dziko lapansi.”+

5 “Tamverani mawu awa amene ndikukuuzani monga nyimbo yoimba polira,+ inu a m’nyumba ya Isiraeli:

 2 “Namwali,+ Isiraeli, wagwa m’dziko lake,+

Iye sangathenso kuimirira.+

Aliyense wamuthawa,

Ndipo palibe womudzutsa.+

3 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti, ‘Mzinda umene unali kupita kukamenya nkhondo ndi anthu 1,000 udzatsala ndi anthu 100, ndipo mzinda umene unali kupita kukamenya nkhondo ndi anthu 100 udzatsala ndi anthu 10. Zimenezi ndi zimene zidzachitikira nyumba ya Isiraeli.’+

4 “Yehova wauza anthu a m’nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yesetsani kundiyandikira,+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+ 5 Musakhale ndi mtima wofuna kupita ku Beteli+ ndipo musabwere ku Giligala.+ Musadutse malire kupita ku Beere-seba+ chifukwa ndithu Giligala adzagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo+ ndipo Beteli adzakhala malo ochitikira zinthu zamatsenga.+ 6 Yesetsani kuyandikira kwa Yehova, inu a m’nyumba ya Yosefe,+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ ndiponso kuti Mulungu asakuyakireni ngati moto.+ Chitani zimenezi kuti motowo usakunyeketseni chifukwa ku Beteli sikungapezeke munthu wouzimitsa.+ 7 Mukuweruza mopanda chilungamo,+ choncho moyo wakhala wowawa ndi wosautsa kwa anthu, pakuti inuyo mwakana chilungamo.+ 8 Yehova ndilo dzina+ la amene anapanga gulu la nyenyezi la Kima+ ndi gulu la nyenyezi la Kesili,+ amene amachititsa mdima wandiweyani+ kukhala kuwala kwa m’mamawa, amenenso amachititsa masana kukhala mdima ngati wausiku,+ amene amaitana madzi akunyanja kuti awakhuthulire panthaka ya dziko lapansi.+ 9 Iye ndiye amabweretsa chiwonongeko mwamsanga pa munthu wamphamvu ngati kuwala kwa mphezi. Ndiponso amachititsa kuti malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri awonongedwe.

10 “‘Anthuwo amadana ndi munthu wowadzudzula pachipata cha mzinda,+ komanso amanyansidwa ndi munthu wowauza chilungamo.+ 11 Inu mukulamula anthu osauka kuti akulipireni mwa kukupatsani zokolola zawo za m’munda, ndiponso kuti azikhoma msonkho mwa kupereka mbewu za m’munda.+ Choncho chifukwa mwachita zinthu zimenezi, simudzapitiriza kukhala m’nyumba zamiyala yosema zimene mwamanga+ ndipo simudzamwa vinyo wochokera m’minda yanu ya mpesa yosiririkayo.+ 12 Pakuti ndadziwa kuchuluka kwa zochita zanu zondipandukira+ ndiponso kukula kwa machimo anu,+ inu amene mukuchitira nkhanza munthu wolungama,+ amene mukulandira ndalama za chitsekapakamwa+ ndiponso amene mukupondereza anthu osauka+ pachipata cha mzinda.+ 13 Choncho, munthu wozindikira adzakhala chete pa nthawi imeneyo chifukwa chakuti idzakhala nthawi yoopsa.+

14 “‘Yesetsani kuchita zabwino osati zoipa+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ ndiponso kuti Yehova Mulungu wa makamu akhale ndi inu monga mmene mwanenera.+ 15 Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.+ Chitani zinthu zachilungamo pachipata cha mzinda,+ mwina Yehova Mulungu wa makamu adzakomera mtima+ otsala a Yosefe.’+

16 “Choncho Yehova, Mulungu wa makamu, Yehova wanena kuti, ‘Padzamveka kulira m’mabwalo onse a mizinda+ yanu ndipo m’misewu yanu yonse anthu azidzanena kuti: “Aa! Aa!” Pamenepo adzaitana mlimi kuti alire+ ndiponso anthu odziwa kulira maliro kuti alire mokweza.’+ 17 ‘Padzakhala kulira mokweza m’minda yonse ya mpesa+ pakuti ine ndidzadutsa pakati panu,’+ watero Yehova.

18 “‘Tsoka kwa anthu amene akulakalaka tsiku la Yehova!+ Kodi mukuyembekezera chiyani pa tsiku la Yehova anthu inu?+ Limeneli lidzakhala tsiku lamdima osati kuwala,+ 19 monga mmene zingakhalire kuti munthu pothawa mkango akukumana ndi chimbalangondo, ndipo pamene akulowa m’nyumba ndi kugwira khoma njoka ikumuluma.+ 20 Tsiku la Yehova lidzakhala lakuda osati lowala, kudzakhaladi mdima osati kuwala.+ 21 Ine ndimadana ndi zikondwerero zanu ndipo ndikuzikana,+ komanso sindidzasangalala ndi fungo la nsembe zanu zoperekedwa pamisonkhano yanu yapadera.+ 22 Inu mukapereka nsembe zathunthu zopsereza,+ ine sindidzasangalala ndi nsembe zanuzo zoperekedwa ngati mphatso,+ ndipo sindidzayang’ana nsembe zanu zachiyanjano zanyama zonenepa.+ 23 Siyani kuimba nyimbo zanu zaphokoso, ndipo sindikufuna kumva nyimbo zanu zoimbidwa ndi zoimbira za zingwe.+ 24 Chilungamo chiyende ngati madzi+ ndiponso ngati mtsinje wosaphwa nthawi zonse.+ 25 Kodi anthu inu a m’nyumba ya Isiraeli, munandipatsa nsembe zanyama ndi zopereka zina pamene munali m’chipululu muja kwa zaka 40?+ 26 Koma inu mudzanyamula Sakuti+ ndi Kaiwani, mafano amene munadzipangira a mulungu wanu wa nyenyezi.+ 27 Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kwambiri ndi ku Damasiko,’+ watero Mulungu wa makamu, amene dzina lake ndi Yehova.”+

6 “Tsoka kwa anthu amene akukhala mwamtendere+ mu Ziyoni ndiponso anthu amene akumva kuti ndi otetezeka m’phiri la Samariya. Iwo ndiwo anthu olemekezeka a mtundu wotchuka pakati pa mitundu ina, ndipo nyumba yonse ya Isiraeli imabwera kwa anthu amenewa. 2 Pitani mukaone ku Kaline ndipo kuchokera kumeneko mukapite ku Hamati+ kumene kuli anthu ambiri, kenako mukapite ku Gati+ wa Afilisiti. Kodi mizinda imeneyi imaposa maufumu anu awiriwa?* Kapena kodi malo awo ndi aakulu kuposa malo anu?+ 3 Kodi inu simukufuna kuganizira za tsiku latsoka?+ Kodi mukufuna kuti chiwawa chizichitika pakati panu?+ 4 Anthu inu mukugona pamipando ya minyanga ya njovu+ ndi kudziwongola pamabedi, ndiponso mukudya nyama ya ana a nkhosa ndi ana amphongo onenepa a ng’ombe zanu.+ 5 Inu mukupeka nyimbo zoti muziimba ndi zipangizo za zingwe,+ ndipo mofanana ndi Davide, mukupanga zipangizo zoimbira.+ 6 Inu mukumwera vinyo m’makapu akuluakulu+ ndipo mukudzola mafuta apamwamba kwambiri+ komanso simunamve ululu pamene tsoka linagwera Yosefe.+

7 “Anthu amenewa adzakhala oyambirira kupita ku ukapolo,+ ndipo phwando laphokoso la anthu ogona modziwongola pamabedi lidzatha.

8 “Yehova, Mulungu wa makamu, wanena kuti: ‘Ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndalumbira pa dzina langa kuti,+ “Ndikunyasidwa ndiponso ndikudana ndi kunyada kwa Yakobo+ ndi nsanja zake zokhalamo,+ chotero ndidzapereka mzindawu ndi zinthu zake zonse kwa adani ake.+ 9 Ngati pangadzatsale anthu 10 m’nyumba imodzi, nawonso adzafa.+ 10 Ndipo m’bale wa bambo ake a mwamuna mmodzi mwa amuna ophedwawo adzawatulutsa ndi kuwatentha mmodzi ndi mmodzi kuti atulutse mafupa onse m’nyumbamo.+ Ndiyeno adzafunsa aliyense amene ali m’chipinda chamkatikati kuti, ‘Kodi muli anthu enanso mmenemo?’ Pamenepo amene ali m’chipindayo adzayankha kuti, ‘Mulibe!’ Kenako adzamuuza kuti, ‘Khala chete! Pakuti ino si nthawi yotchula dzina la Yehova.’”+

11 “‘Tsopano Yehova akalamula,+ nyumba zikuluzikulu zigwetsedwa n’kusanduka mulu wa dothi ndipo nyumba zing’onozing’ono zisanduka zibuma zokhazokha.+

12 “‘Kodi mahatchi angathamange pathanthwe, kapena kodi munthu angalime pathanthwe ndi ng’ombe? Anthu inu mwakana chilungamo,+ choncho mwachititsa moyo wa anthu kukhala wowawa. 13 Inu mukusangalala ndi chinthu chimene palibe+ ndipo mukunena kuti: “Tadzipezera tokha mphamvu.”’*+ 14 Tsopano Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti, ‘Inu a m’nyumba ya Isiraeli, ine ndikukudzutsirani mtundu wa anthu+ umene udzakuponderezani kuyambira kumalire ndi Hamati+ mpaka kuchigwa cha Araba.’”

7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinamuona akutumiza dzombe, anthu atatsala pang’ono kubzala mbewu zomaliza.+ Nthawi imeneyi inali yobzala mbewu zomaliza, anthu atamweta udzu wopita kwa mfumu. 2 Ndiyeno dzombelo litamaliza kudya zomera zonse za m’dziko, ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde khululukani.+ Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji, pakuti ndi wamng’ono?”+

3 Yehova anamva chisoni+ ndipo Yehova anati, “Zimenezi sizidzachitika.”

4 Kenako, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsanso masomphenya awa: Ndinaona Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuuza anthu ake kuti alimbane naye pogwiritsira ntchito moto.+ Motowo unaumitsa madzi akuya ndiponso unawononga kachigawo ka dziko. 5 Ndiyeno ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde musatero.+ Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji, pakuti ndi wamng’ono?”+

6 Pamenepo Yehova anamva chisoni+ ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anati, “Zimenezinso sizidzachitika.”

7 Kenako, iye anandionetsanso masomphenya awa: Ndinaona Yehova ataima pamwamba pa khoma limene linamangidwa pogwiritsa ntchito chingwe chowongolera,+ ndipo iye anali ndi chingwe chowongolera m’dzanja lake. 8 Ndiyeno Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Amosi?” Ndinamuyankha kuti: “Ndikuona chingwe chowongolera.” Pamenepo Yehova anati: “Ine ndiika chingwe chowongolera pakati pa anthu anga Aisiraeli,+ ndipo sindidzawakhululukiranso.+ 9 Malo okwezeka a Isaki+ adzawonongedwa, ndipo malo opatulika+ a Isiraeli nawonso adzasakazidwa.+ Ine ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu* ndi lupanga.”+

10 Ndiyeno Amaziya wansembe wa ku Beteli,+ anatumiza uthenga kwa Yerobowamu+ mfumu ya Isiraeli kuti: “Amosi wakukonzerani chiwembu mkati mwenimweni mwa Isiraeli,+ ndipo anthu atopa nawo mawu akewo.+ 11 Amosi wanena kuti, ‘Yerobowamu adzaphedwa ndi lupanga, ndipo mosalephera Isiraeli adzagwidwa m’dziko lake ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.’”+

12 Ndiyeno Amaziya anauza Amosi kuti: “Iwe wamasomphenya,+ choka, thawira kudziko la Yuda, ndipo kumeneko uzikadya mkate ndi kunenera. 13 Koma usapitirize kunenera ku Beteli kuno,+ pakuti ndi malo opatulika a mfumu,+ ndiponso Beteli ndi nyumba ya ufumu uno.”

14 Pamenepo Amosi anayankha Amaziya kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri,+ koma ndinali m’busa+ ndiponso woboola nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga kumene ndinali kuweta nkhosa, ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisiraeli.’+ 16 Tsopano mvera mawu a Yehova, ‘Kodi iwe ukundiuza kuti: “Usanenere zinthu zoipa zokhudza Isiraeli,+ ndipo usatchule mawu alionse oipa+ okhudza nyumba ya Isaki”? 17 Yehova wanena kuti: “Mkazi wako adzakhala hule mumzindawu.+ Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Anthu adzagawana dziko lako mochita kuyeza ndi chingwe, ndipo iweyo udzafera m’dziko lodetsedwa.+ Ndithudi, Isiraeli adzagwidwa m’dziko lake ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.”’”+

8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinaona dengu la zipatso za m’chilimwe.*+ 2 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani+ Amosi?” Ndinayankha kuti: “Ndikuona dengu la zipatso za m’chilimwe.”+ Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Mapeto afika pa anthu anga Aisiraeli.+ Sindidzawamveranso chisoni.+ 3 ‘Pa tsiku limenelo nyimbo za m’kachisi zidzasanduka kulira kofuula,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Padzakhala mitembo yambiri+ ndipo munthu adzataya mitemboyo panja, pamalo pena paliponse, moti kudzangoti zii!’

4 “Tamverani izi amuna inu, inu amene mukufuna kumeza munthu wosauka+ ndiponso amene mukufuna kufafaniza anthu ofatsa padziko lapansi.+ 5 Inu mukunena kuti: ‘Kodi mwezi watsopano utha liti+ kuti tiyambe kugulitsa chakudya?*+ Komanso sabata+ litha liti kuti tiyambe kuchepetsa muyezo wogulitsira zinthu,+ kukweza mtengo ndi kubera wogula mwa kugwiritsa ntchito masikelo achinyengo?+ 6 Kodi sabata litha liti kuti tigule anthu onyozeka ndi ndalama zasiliva, kuti tigule munthu wosauka pa mtengo wa nsapato ndiponso kuti tigulitse mbewu zachabechabe?’+

7 “Yehova, amene ndi ulemerero wa Yakobo, walumbira pa dzina lake+ kuti, ‘Sindidzaiwala ntchito zawo zonse.+ 8 Pa chifukwa chimenechi dziko lidzagwedezeka,+ ndipo aliyense wokhala mmenemo adzalira.+ Dziko lonselo lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo ndi kuwinduka, ndipo kenako lidzaphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.’+

9 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo ndidzachititsa kuti dzuwa lilowe masanasana,+ ndiponso kuti m’dziko mugwe mdima dzuwa lisanalowe. 10 Ndidzasandutsa zikondwerero zanu kukhala maliro+ ndipo nyimbo zanu zonse zidzakhala nyimbo zoimba polira. Ndidzachititsa kuti anthu onse avale ziguduli* ndipo mitu yonse idzametedwa mpala.+ Ndidzachititsa kuti zochitika pa tsikulo zikhale ngati maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo amene wamwalira,+ moti tsiku la mapeto a zinthu zonsezi lidzakhala lowawa.’

11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani, masiku akubwera pamene ndidzatumiza njala m’dziko. Njala imeneyo siidzakhala ya chakudya kapenanso ludzu lofuna madzi ayi, koma idzakhala njala ndiponso ludzu lofuna kumva mawu a Yehova.+ 12 Anthu adzayenda modzandira kuchokera kunyanja mpaka kukafika kunyanja, kuchokera kumpoto mpaka kukafika kum’mawa. Iwo adzakhala akuyendayenda pofunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza.+ 13 Pa tsiku limenelo anamwali okongola ndiponso anyamata adzakomoka chifukwa cha ludzu.+ 14 Iwo amalumbira pa milungu yonama ya ku Samariya,*+ ya ku Dani,+ ndi ya ku Beere-seba.*+ Ndithu, anthu amenewa adzagwa ndipo sadzadzukanso.’”+

9 Ndinaona Yehova ataima pamwamba pa guwa lansembe,+ ndipo anati: “Menya mutu wa chipilala kuti maziko ake agwedezeke ndipo udulenso mitu ya zipilala zonse.+ Ndiyeno otsala mwa anthuwo ndidzawapha ndi lupanga. Aliyense wa iwo amene adzathawa ndidzamuphabe, aliyense wa iwo amene adzathawa sadzapulumuka.+ 2 Akakumba Manda* kuti abisale mmenemo ndidzawatulutsa ndi dzanja langa,+ ndipo akakwera kumwamba ndidzawatsitsira pansi.+ 3 Akabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, ndidzawafufuza mosamala ndi kuwatenga,+ ndipo akathawa pamaso panga ndi kubisala pansi pa nyanja,+ ndidzalamula njoka pansi pa nyanja pomwepo kuti iwalume. 4 Akatengedwa ndi adani awo kupita ku ukapolo, kumeneko ndidzalamula lupanga kuti liwaphe.+ Ndidzakhala tcheru kuti ndiwagwetsere tsoka osati kuwapatsa madalitso.+ 5 Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, ndiye amasungunula dziko mwa kungolikhudza.+ Onse okhala mmenemo adzalira.+ Dziko lonse lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo, ndipo kenako lidzaphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.+

6 “‘Yehova ndilo dzina+ la amene amamanga makwerero ake kumwamba+ ndi kumanganso nyumba pamwamba pa dziko lapansi limene analikhazikitsa,+ amene amaitana madzi akunyanja+ kuti awakhuthulire panthaka ya dziko lapansi.’+

7 “Yehova akufunsa kuti, ‘Inu ana a Isiraeli, kodi simuli ngati ana a Akusi kwa ine? Kodi si ndine amene ndinatulutsa Aisiraeli m’dziko la Iguputo,+ amenenso ndinatulutsa Afilisiti+ ku Kerete komanso Asiriya ku Kiri?’+

8 “Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyang’ana ufumu wochimwawo,+ ndipo ndidzaufafaniza panthaka ya dziko lapansi.+ Komabe nyumba ya Yakobo+ sindidzaifafaniza yonse. 9 Pakuti taonani, ine ndalamula kuti nyumba ya Isiraeli igwedezedwe pakati pa mitundu yonse,+ monga mmene munthu amachitira posefa, ndipo mwala sudzadutsa kuti ugwere pansi. 10 Anthu anga onse ochimwa adzaphedwa ndi lupanga.+ Iwo amanena kuti: “Tsoka silitiyandikira kapena kutigwera.”’+

11 “‘Pa tsiku limenelo, ndidzautsa+ nyumba+ ya Davide imene inagwa,+ ndi kukonza mmene khoma* lake linawonongeka. Ndidzautsa mabwinja ake ndipo ndidzaimanga kuti ikhale ngati masiku akale.+ 12 Ndidzachita zimenezi kuti anthu anga adzatenge zinthu zotsala za Edomu+ ndi mitundu yonse ya anthu imene inali kuitanira pa dzina langa,’+ watero Yehova, amene akuchita zimenezi.

13 “Yehova wanena kuti, ‘Masiku adzafika pamene wolima adzapitirira wokolola,+ ndipo woponda mphesa adzapitirira munthu amene wanyamula mbewu zoti akabzale.+ Mapiri adzachucha vinyo wotsekemera*+ ndipo zitunda zonse zidzatulutsa vinyo wochuluka.+ 14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+

15 “‘Ine ndidzawabzala panthaka yawo ndipo sadzazulidwanso m’dziko limene ndawapatsa,’+ watero Yehova Mulungu wanu.”

Mawu ake enieni, “Chifukwa cha kupanduka katatu ndiponso chifukwa cha kupanduka kanayi.”

Ena amati “hosi,” kapena “kavalo.”

Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”

Mawu ake enieni, “ndinakupatsani mano oyera.”

Amenewa ndi maufumu a Yuda ndi Isiraeli.

Mawu ake enieni, “Tadzitengera nyanga.”

Ameneyu ndi Yerobowamu Wachiwiri, mwana wa Yowasi (Yehowasi). Onani Amo 1:1.

Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina zipatso za kanjedza.

Pamenepa mwina anali kutanthauza tirigu kapena barele.

Ena amati “masaka.”

M’Chiheberi, “amalumbira pa tchimo la Samariya,” kutanthauza mafano a ku Samariya amene anawachititsa tchimolo.

M’Chiheberi, “njira ya ku Beere-seba.” Mwina kutanthauza njira imene anali kuyendamo popita kukapembedza milungu yonama kumeneko.

Onani Zakumapeto 5.

Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”

Ena amati “wonzuna.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena