YOBU
1 Mʼdziko la Uzi munali munthu wina dzina lake Yobu.*+ Iye anali munthu wokhulupirika amene ankachita zoyenera,*+ ankaopa Mulungu ndiponso ankapewa zoipa.+ 2 Yobu anali ndi ana aamuna 7 komanso ana aakazi atatu. 3 Iye anali ndi nkhosa 7,000, ngamila 3,000, ngʼombe 1,000 ndi abulu 500.* Analinso ndi antchito ambiri, moti anali munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kumʼmawa.
4 Mwana wake aliyense wamwamuna ankakonza phwando kunyumba kwake pa tsiku limene wasankha.* Iwo ankaitana azichemwali awo atatu kuti adzadye ndi kumwera limodzi. 5 Akamaliza kuchita maphwando kunyumba zawo zonse, Yobu ankawaitana kuti adzawayeretse. Kenako iye ankadzuka mʼmamawa kwambiri nʼkuperekera mwana aliyense nsembe zopsereza.+ Chifukwa iye ankati: “Mwina ana anga achimwa ndipo anyoza Mulungu mumtima mwawo.” Izi ndi zimene Yobu ankachita nthawi zonse.+
6 Tsopano linafika tsiku limene ana a Mulungu woona*+ anapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo Satana+ nayenso anafika pakati pawo.+
7 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anayankha Yehova kuti: “Ndimazungulira mʼdziko lapansi komanso kuyendayendamo.”+ 8 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe wina wofanana naye. Iye ndi munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera,*+ amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa.” 9 Ndiyeno Satana anayankha Yehova kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu popanda chifukwa?+ 10 Kodi inuyo simwamuteteza pomuikira mpanda?+ Mwatetezanso nyumba yake ndi zinthu zonse zimene ali nazo. Mwadalitsa ntchito ya manja ake+ ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri mʼdzikoli. 11 Koma panopa mutambasule dzanja lanu nʼkuwononga zinthu zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani mʼmaso muli gwa!” 12 Kenako Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, chilichonse chimene ali nacho chili mʼmanja mwako. Koma dzanja lako lisakhudze munthuyo.” Zitatero Satana anachoka pamaso pa Yehova.+
13 Tsopano pa tsiku limene ana a Yobu, aamuna ndi aakazi, ankadya komanso kumwa vinyo mʼnyumba ya mchimwene wawo wamkulu,+ 14 kunabwera munthu kwa Yobu kudzanena uthenga wakuti: “Ngʼombe zimalima ndipo abulu amadya msipu chapambali pake. 15 Kenako Asabeya anabwera nʼkutiukira ndipo analanda ziweto nʼkupha atumiki anu ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.”
16 Asanamalize kulankhula, munthu wina anabwera nʼkunena kuti: “Moto wa Mulungu unatsika* kuchokera kumwamba, ndipo unayaka pakati pa nkhosa ndi atumiki anu moti nkhosa komanso atumiki anuwo apsa. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.”
17 Asanamalize kulankhula, munthu winanso anabwera nʼkudzanena kuti: “Akasidi+ anapanga magulu atatu ndipo anaukira ngamila zanu nʼkuzitenga, komanso apha atumiki anu ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.”
18 Asanamalize kulankhula, kunabwera munthu winanso kudzanena kuti: “Ana anu aamuna ndi aakazi amadya komanso kumwa vinyo mʼnyumba ya mchimwene wawo wamkulu. 19 Mwadzidzidzi kunabwera chimphepo kuchokera mʼchipululu ndipo chinawomba makona 4 a nyumbayo, moti nyumbayo yagwera ana anu nʼkuwapha. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.”
20 Yobu atamva zimenezi anaimirira nʼkungʼamba chovala chake ndiponso kumeta tsitsi kumutu kwake. Kenako anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi 21 nʼkunena kuti:
“Ndinatuluka mʼmimba mwa mayi anga ndili wamaliseche,
Ndipo ndidzabwerera ndilinso wamaliseche.+
Yehova wapereka,+ ndipo Yehova yemweyo watenga.
Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.”
22 Ngakhale kuti anakumana ndi zinthu zonsezi, Yobu sanachimwe kapena kuimba Mulungu mlandu woti wachita zinthu zoipa.*
2 Pambuyo pa zimenezi, linafika tsiku limene ana a Mulungu woona*+ anapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo Satana nayenso anapita kukaonekera pamaso pa Yehova.+
2 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anayankha Yehova kuti: “Ndimazungulira mʼdziko lapansi komanso kuyendayendamo.”+ 3 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe wina wofanana naye. Iye ndi munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera,*+ amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa. Iye akupitirizabe kukhala wokhulupirika+ ngakhale kuti iweyo ukufuna kuti ndimuwononge*+ popanda chifukwa.” 4 Koma Satana anayankha Yehova kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake. 5 Koma panopa mutambasule dzanja lanu nʼkuwononga thupi lake,* ndipo akutukwanani mʼmaso muli gwa!”+
6 Ndiyeno Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, iye ali mʼmanja mwako. Koma usachotse moyo wake.” 7 Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova nʼkukachititsa kuti Yobu azunzike ndi zilonda zopweteka,+ kuyambira kuphazi mpaka kumutu. 8 Ndiyeno Yobu anatenga phale loti azidzikandira ndipo ankakhala paphulusa.+
9 Patapita nthawi, mkazi wake anamufunsa kuti: “Kodi mukupitirizabe kukhala wokhulupirika? Tukwanani Mulungu mufe!” 10 Koma Yobu anamuyankha kuti: “Ukulankhula ngati mmene amalankhulira akazi opusa. Kodi tizingolandira zabwino zokhazokha kuchokera kwa Mulungu woona osalandiranso zoipa?”+ Ngakhale kuti anakumana ndi zonsezi, Yobu sananene chilichonse cholakwika.*+
11 Anzake atatu a Yobu anamva za masoka onse amene anamugwera ndipo aliyense wa iwo anabwera kuchokera kwawo. Mayina awo anali Elifazi+ wa ku Temani, Bilidadi+ wa ku Shuwa+ ndi Zofari+ wa ku Naama. Iwo anapangana kuti akumane kuti apite akatonthoze Yobu ndi kumulimbikitsa. 12 Atamuona ali chapatali, sanamuzindikire. Kenako anayamba kulira mokweza mawu ndipo anangʼamba zovala zawo nʼkumawaza fumbi mʼmwamba komanso pamutu pawo.+ 13 Kenako anakhala pansi limodzi ndi Yobuyo kwa masiku 7 masana ndi usiku. Palibe amene analankhula naye chilichonse chifukwa anaona kuti ululu wake unali waukulu kwambiri.+
3 Pambuyo pa zimenezi mʼpamene Yobu anayamba kulankhula ndi kutemberera tsiku limene anabadwa.*+ 2 Yobu anati:
3 “Zikanakhala bwino tsiku limene ndinabadwa likanapanda kufika,+
Ndiponso usiku umene wina ananena kuti: ‘Mwamuna wapangika mʼmimba.’
4 Tsiku limenelo likhale mdima.
Mulungu wakumwamba asaliganizirenso,
Ndipo kuwala kusalifikire.
5 Mdima wandiweyani ulitenge.*
Mtambo wa mvula uliphimbe.
Zinthu zimene zimadetsa tsiku ziliopseze.
6 Usiku umenewo utengedwe ndi mdima wandiweyani.+
Usasangalale pakati pa masiku apachaka,
Pachiwerengero cha miyezi, usalowe nawo.
7 Ndithu usiku umenewo ukhale wosabereka.
Phokoso lachisangalalo lisamveke usiku umenewo.
8 Otemberera masiku alitemberere tsikulo,
Iwo amene angathe kudzutsa ngʼona.+
9 Nyenyezi zake zamʼmawa kuli kachisisira zizime.
Lidikire kuwala koma lisakuone,
Ndipo lisaone kuwala kwa mʼbandakucha.
10 Chifukwa silinatseke zitseko za mimba ya mayi anga,+
Komanso silinabise mavuto kuti ndisawaone.
11 Nʼchifukwa chiyani sindinafe pobadwa?
Nʼchifukwa chiyani sindinamwalire nditatuluka mʼmimba?+
12 Nʼchifukwa chiyani mawondo a mayi anga anandilandila,
Ndipo nʼchifukwa chiyani anandiyamwitsa?
13 Chifukwa pano bwenzi ndikugona popanda wondisokoneza.+
Bwenzi ndili mʼtulo komanso ndikupuma+
14 Limodzi ndi mafumu apadziko lapansi ndi alangizi awo,
Amene anadzimangira malo omwe panopa ndi mabwinja.
15 Kapena ndi akalonga amene anali ndi golide,
Amene nyumba zawo zinadzaza ndi siliva.
16 Kapena nʼchifukwa chiyani sindinakhale ngati pakati pomwe papita padera popanda mayi kuzindikira,
Ngati ana amene sanaonepo kuwala?
17 Ngakhale oipa asiya kuvutika kumandako,
Ndipo kumeneko anthu ofooka, akupuma.+
18 Kumeneko akaidi onse ali pa mtendere.
Iwo samvanso mawu a munthu wowakakamiza kugwira ntchito.
19 Anthu onyozeka ndi olemekezeka amakhala chimodzimodzi kumeneko,+
Ndipo kapolo amamasuka kwa mbuye wake.
20 Nʼchifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene akuvutika,
Ndiponso moyo kwa anthu omwe ali pamavuto aakulu?+
21 Nʼchifukwa chiyani anthu amene amafuna kufa, samafa?+
Iwo amakumba pansi pofunafuna imfa, kuposa mmene amakumbira chuma chobisika.
22 Anthu amenewa amasangalala kwambiri,
Amakondwera akapeza manda.
23 Nʼchifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene wasochera,
Amene Mulungu wamutchingira njira?+
24 Chifukwa mʼmalo moti ndidye chakudya ndimausa moyo,+
Ndipo kubuula kwanga+ kumakhuthuka ngati madzi.
25 Chifukwa chinthu chimene ndimachita nacho mantha chandibwerera,
Ndipo chimene ndinali kuchiopa chandichitikira.
26 Ndikusowa mtendere, mavuto achuluka, sindikupeza mpumulo,
Koma mavuto akungobwerabe.”
4 Kenako Elifazi+ wa ku Temani anayankha kuti:
2 “Munthu atayesa kukulankhula, kodi sukhumudwa?
Chifukwa ndi ndani angathe kudziletsa kuti asalankhule?
3 Nʼzoona kuti walangiza anthu ambiri,
Ndipo unkalimbitsa anthu ofooka.
4 Mawu ako ankadzutsa munthu aliyense amene wagwa,
Ndipo unkalimbitsa anthu amene mawondo awo anali olobodoka.
5 Koma panopa zakuchitikira iweyo, ndipo watopa nazo,
Zakhudza iweyo, ndipo wafooka nazo.
6 Popeza umaopa Mulungu, kodi sukuyenera kulimba mtima?
Popeza ndiwe wokhulupirika,+ kodi ulibe chiyembekezo?
7 Takumbukira: Kodi pali munthu wosalakwa amene anawonongedwapo?
Ndi liti pamene anthu ochita zoyenera anawonongedwapo?
8 Zimene ine ndaona nʼzakuti, anthu amene amalima* munda wa zoipa,
Ndiponso amene amafesa mavuto, amakolola zomwezo.
9 Iwo amawonongeka ndi mpweya wa Mulungu,
Ndipo mkwiyo wake ukayaka amatha.
10 Mkango umabangula, ndipo mkango wamphamvu umamveka kulira,
Komabe ngakhale mano a mikango yamphamvu,* amathyoka.
11 Mkango umafa chifukwa chosowa nyama yoti udye,
Ndipo ana a mkango amamwazikana.
12 Tsopano winawake anandibweretsera mawu mwachinsinsi,
Ndipo khutu langa linamva kunongʼona kwa mawuwo.
13 Maganizo osautsa atandifikira mʼmasomphenya usiku,
Pa nthawi imene anthu amakhala ali mʼtulo tofa nato,
14 Ndinanjenjemera kwambiri,
Ndipo mafupa anga onse anagwidwa ndi mantha.
15 Mzimu unadutsa kumaso kwanga,
Ndipo ubweya wa pathupi langa unaimirira.
16 Kenako mzimuwo unaima,
Koma sindinazindikire maonekedwe ake.
Chinthu chinaima pamaso panga.
Kunali bata, kenako ndinamva mawu akuti:
17 ‘Kodi munthu angakhale wolungama kuposa Mulungu?
Kodi munthu angakhale woyera kuposa amene anamupanga?’
18 Iyetu sakhulupirira atumiki ake,
Ndipo angelo* ake amawapezera zifukwa.
19 Nanga kuli bwanji anthu amene amakhala mʼnyumba zadothi,
Amene maziko awo ali mʼfumbi?+
Amene amathudzulidwa mosavuta ngati kadziwotche.
20 Amakhala ndi moyo mʼmawa koma pofika madzulo amakhala ataphwanyika.
Amawonongeka kwamuyaya, ndipo palibe amene amazindikira.
21 Iwo ali ngati tenti imene chingwe chake chasololedwa.
Iwo amafa alibe nzeru.”
5 “Taitana! Kodi pali aliyense amene akukuyankha?
Ndipo kodi utembenukira kwa mngelo* uti?
2 Chifukwa kusunga chakukhosi kudzapha wopusa,
Ndipo nsanje idzapha munthu amene sachedwa kukopeka.
3 Ine ndaonapo wopusa atazika mizu,
Koma mwadzidzidzi malo ake okhala anatembereredwa.
4 Ana ake ndi osatetezeka,
Ndipo amaponderezedwa pageti la mzinda,+ popanda wowapulumutsa.
5 Munthu wanjala amadya zimene munthu wopusa wakolola,
Iye amatenga ngakhale zimene zamera paminga,
Ndipo chuma cha munthu wopusayo ndi ana ake chimalandidwa.
6 Zinthu zoipa siziphuka kuchokera mufumbi,
Ndipo mavuto satuluka munthaka.
7 Chifukwa munthu amabadwa kuti akumane ndi mavuto,
Ngati mmene moto umathethekera kupita mʼmwamba.
8 Koma ndikanakhala ine, ndikanakadandaula kwa Mulungu,
Ndipo ndikanakatula mlandu wanga kwa Mulunguyo,
9 Kwa Iye amene amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,
Zinthu zodabwitsa zosawerengeka.
10 Iye amapereka mvula padziko lapansi,
Ndipo amapititsa madzi kuminda.
11 Iye amakweza munthu wonyozeka pamwamba,
Ndipo amapulumutsa munthu amene akuvutika.
12 Iye amalepheretsa zolinga za anthu ochenjera,
Nʼcholinga choti ntchito ya manja awo isayende bwino.
13 Iye amachititsa kuti anzeru agwere mʼmisampha yawo,+
Kuti mapulani a anthu ochenjera alephereke.
14 Iwo amakumana ndi mdima masana,
Ndipo amapapasa masana ngati kuti ndi usiku.
15 Iye amapulumutsa munthu ku lupanga lochokera mʼkamwa mwa oipa,
Amapulumutsa wosauka mʼmanja mwa munthu wamphamvu,
16 Kuti wonyozeka akhale ndi chiyembekezo,
Koma pakamwa pa anthu opanda chilungamo pamatsekedwa.
17 Tamvera! Wosangalala ndi munthu amene Mulungu amamudzudzula.
Choncho usakane chilango* cha Wamphamvuyonse.
18 Chifukwa iye amapangitsa kuti munthu amve kupweteka, koma amamanga chilonda chopwetekacho.
Amaphwanya anthu, koma amawachiritsa ndi manja ake.
19 Adzakupulumutsa ku masoka 6,
Ndipo ngakhale tsoka la 7 silidzakuvulaza.
20 Pa nthawi yanjala adzakupulumutsa* ku imfa,
Ndipo adzakupulumutsa ku mphamvu ya lupanga pa nthawi yankhondo.
21 Mulungu adzakuteteza ku lilime lomenya ngati chikwapu,+
Ndipo sudzachita mantha tsoka likadzafika.
22 Sudzada nkhawa ndi masoka kapena njala,
Ndipo sudzaopa nyama zakutchire.
23 Miyala yakutchire sidzakuvulaza,*
Ndipo nyama zakutchire zidzakhala nawe mwamtendere.
24 Udzaona kuti tenti yako ndi yotetezeka,*
Ndipo ukamayendera malo ako odyetserako ziweto, udzaona kuti palibe chimene chikusowa.
25 Udzasangalala kuona ana ako atachuluka,
Ndipo mbadwa zako zidzakhala zochuluka ngati zomera za padziko lapansi.
26 Udzakhalabe ndi mphamvu ukamadzalowa mʼmanda,
Mofanana ndi ngala za tirigu zimene zakololedwa pa nyengo yake.
27 Izi nʼzimene tafufuza ndipo zilidi choncho.
Imva zimenezi ndipo uzivomereze.”
6 Ndiyeno Yobu anayankha kuti:
2 “Zikanakhala bwino mavuto+ anga onse akanayezedwa kulemera kwake,
Nʼkuikidwa pasikelo limodzi ndi masautso anga.
3 Chifukwa panopa akulemera kuposa mchenga wamʼnyanja.
Nʼchifukwa chake ndalankhula mosaganiza bwino.*+
4 Chifukwa mivi ya Wamphamvuyonse yandilasa,
Ndipo ine ndikumwa poizoni wa miviyo.+
Mulungu akundiukira ndipo ndikuchita mantha kwambiri.
5 Kodi bulu wamʼtchire+ amalira ndi njala ali ndi msipu?
Kapena kodi ngʼombe yamphongo imalira ili ndi chakudya?
6 Kodi chakudya chosakoma chingadyedwe chopanda mchere?
Kapena kodi utomoni wa zomera umakoma?
7 Ndakana kukhudza zinthu zimenezi.
Zili ngati chakudya chowonongeka.
8 Zikanakhala bwino zimene ndapempha zikanachitika,
Ndiponso Mulungu akanandipatsa zimene ndikufuna.
9 Zikanakhala bwino Mulungu akanati angondiphwanya,
Akanati atambasule dzanja lake nʼkundipha.+
10 Ngakhale zimenezo, zikanatha kunditonthoza.
Ndikanadumpha ndi chisangalalo ngakhale kuti ndikumva ululu wosaneneka,
Chifukwa sindinakane mawu a Woyerayo.+
11 Kodi ndili ndi mphamvu kuti ndipitirize kudikira?+
Ndipo kodi ndili ndi chiyembekezo chilichonse kuti ndipitirizebe kukhala ndi moyo?*
12 Kodi mphamvu zanga ndi zofanana ndi za thanthwe?
Kapena kodi mnofu wanga ndi wopangidwa ndi kopa?*
13 Kodi pali chimene ndingachite kuti ndidzithandize,
Pamene zinthu zonse zimene zinkandithandiza zachotsedwa kwa ine?
15 Abale anga enieni akhala osadalirika+ ngati mtsinje umene umayenda madzi nthawi ya mvula yokha,
Umene umauma mvula ikatha.
16 Iwo ali ngati mitsinje imene imakhala ndi madzi akuda chifukwa cha matope,
Amene amabwera madzi oundana akasungunuka.
17 Koma pakapita nthawi imakhala yopanda madzi ndipo imatha.
Kukatentha, imauma.
18 Njira zake ndi zokhotakhota.
Mitsinjeyo imapita kuchipululu kenako nʼkuuma.
20 Amachita manyazi chifukwa amakhulupirira kuti apeza madzi,
Koma akafikapo amakhumudwa.
21 Mofanana ndi zimenezi, ndi mmene inu mulili kwa ine.+
Mwaona kuopsa kwa mavuto amene ndakumana nawo ndipo mwachita mantha.+
22 Kodi ndanena kuti, ‘Ndipatseni kanthu,’
Kapena kodi ndapempha kuti mundiperekere mphatso kuchokera pa chuma chanu?
23 Kodi ndapempha kuti mundipulumutse mʼmanja mwa mdani,
Kapena kuti mundilanditse* mʼmanja mwa anthu ankhanza?
24 Ndilangizeni, ndipo ine ndikhala chete.+
Ndithandizeni kuti ndimvetse zimene ndalakwitsa.
25 Munthu akamanena zoona, sizipweteka.+
Koma kodi kudzudzula kwanu kuli ndi phindu lanji?+
26 Kodi mwapangana kuti mudzudzule mawu anga,
Mawu a munthu amene wasokonezeka maganizo,+ omwe amatengedwa ndi mphepo?
28 Tsopano tembenukani ndipo mundiyangʼane,
Chifukwa sindingakunamizeni.
29 Chonde ganizirani mofatsa, musandiweruze molakwa.
Ndithu ganizirani mofatsa, chifukwatu ine ndikadali wolungama.
30 Kodi lilime langa likulankhula zinthu zopanda chilungamo?
Kodi mʼkamwa mwanga simuzindikira kuti chinachake chalakwika?”
7 “Kodi moyo wa munthu padziko lapansi suli ngati ntchito yokakamiza?
Ndipo kodi masiku ake sali ngati masiku a munthu waganyu?+
2 Mofanana ndi kapolo, iye amalakalaka mthunzi,
Ndipo mofanana ndi munthu waganyu, iye amadikirira malipiro ake.+
3 Choncho kwa miyezi yambiri moyo wanga wakhala wachabechabe
Ndipo usiku wambiri ndimakhala ndikuvutika.+
4 Ndikagona ndimafunsa kuti, ‘Kodi kucha nthawi yanji?’+
Usikuwo umatalika ndipo ndimangotembenukatembenuka mpaka mʼbandakucha.
6 Masiku anga akuthamanga kuposa mashini owombera nsalu,+
Atha mofulumira ndipo ine ndilibe chiyembekezo.+
7 Kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mphepo,+
Ndiponso kuti diso langa silidzaonanso zinthu zosangalatsa.*
8 Diso limene likundiona panopa silidzandionanso,
Mudzandifunafuna, koma ine kudzakhala kulibe.+
10 Iye sadzabwereranso kunyumba yake,
Ndipo anthu a pamalo ake sadzamukumbukiranso.+
11 Choncho, ine sinditseka pakamwa panga.
Ndilankhula chifukwa cha ululu umene ndikumva mumtima mwanga,
Ndidandaula mopwetekedwa mtima.+
12 Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cha mʼnyanja,
Kuti mundiikire mlonda?
13 Ndikanena kuti, ‘Bedi langa linditonthoza,
Bedi langa lindithandiza kuchepetsako chisoni changa,’
14 Inuyo mumandiopseza ndi maloto,
Ndipo mumandichititsa mantha ndi masomphenya.
15 Choncho ndikulakalaka kufa chifukwa chobanika,
Kulibwino ndife kusiyana nʼkuti thupi langa likhale chonchi.+
16 Moyo wanga ndikunyansidwa nawo,+ sindikufuna kupitirizanso kukhala ndi moyo.
Ndisiyeni, chifukwa masiku anga ali ngati mpweya wotuluka mʼmphuno.+
18 Nʼchifukwa chiyani mumamuyendera mʼmawa uliwonse,
Nʼkumamuyesa nthawi zonse?+
19 Nʼchifukwa chiyani simukusiya kundiyangʼana,
Nʼkundipatsa nthawi yokwanira kuti ndingomezako malovu?+
20 Ngati ndachimwa, kodi zimakukhudzani bwanji, Inu amene mumayangʼanitsitsa anthu?+
Nʼchifukwa chiyani mukulimbana ndi ine?
Kodi ndakhala mtolo wolemera kwa inu?
21 Nʼchifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga,
Nʼkunyalanyaza zolakwa zanga?
Chifukwa posachedwapa ndigona mʼfumbi,+
Ndipo mudzandifunafuna koma ine kudzakhala kulibe.”
8 Bilidadi+ wa ku Shuwa+ anayankha kuti:
2 “Kodi ukhala ukulankhula chonchi mpaka liti?+
Mawu a mʼkamwa mwako ali ngati mphepo yamphamvu.
3 Kodi Mulungu angapotoze chilungamo?
Kapena kodi Wamphamvuyonse angapotoze zinthu zimene ndi zolungama?
4 Ngati ana ako anamuchimwira,
Iye anawalanga chifukwa cha kupanduka kwawo,*
5 Koma ngati iweyo utayangʼana kwa Mulungu,+
Nʼkuchonderera Wamphamvuyonse kuti akuchitire chifundo,
6 Ndipo ngati ukanakhaladi woyera komanso ngati umachitadi zoyenera,+
Iye akanakumvera*
Ndipo akanakubwezeretsa mmene unalili poyamba.
7 Ndipo ngakhale kuti chiyambi chako chinali chachingʼono,
Tsogolo lako likanakhala lalikulu.+
8 Tafunsa mʼbadwo wakale,
Ndipo ganizira zinthu zimene makolo awo anapeza.+
9 Chifukwa ife tabadwa dzulodzuloli, ndipo sitikudziwa kalikonse,
Chifukwa masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi.
10 Kodi iwo sadzakulangiza
Ndipo sadzakuuza zimene akudziwa?*
11 Kodi gumbwa* angamere pamalo pamene si padambo?
Ndipo kodi bango lingakule popanda madzi?
12 Lidakali ndi maluwa, lisanadulidwe nʼkomwe,
Lidzauma zomera zonse zisanaume.
13 Zimenezi ndi zimene zidzachitikire* anthu onse amene aiwala Mulungu,
Chifukwa chiyembekezo cha anthu oipa* chidzatha.
14 Amene amadalira zinthu zosathandiza,
Amene amadalira zinthu zosalimba ngati ulusi wa kangaude.*
15 Iye adzatsamira nyumba yake, koma idzagwa.
Adzayesetsa kuigwira, koma sidzalimba.
16 Iye ali ngati chomera chothiriridwa chimene chili padzuwa.
Ndipo nthambi zake zimakula mʼmunda.+
17 Mizu yake imapiringizana pamulu wa miyala.
Iye amaona kuti miyalayo ndi nyumba yake.
20 Ndithudi, Mulungu sadzakana anthu okhulupirika,*
Kapena kuthandiza* anthu ochita zoipa.
21 Chifukwa adzakupangitsa kuti useke,
Ndipo udzafuulanso chifukwa chosangalala.
22 Anthu odana nawe adzachita manyazi,
Ndipo tenti ya anthu oipa kudzakhala kulibe.”
9 Yobu anayankha kuti:
2 “Ndikudziwa ndithu kuti zili choncho.
Koma kodi munthu anganene bwanji kuti ndi wosalakwa pamaso pa Mulungu?+
3 Ngati munthu akufuna kutsutsana ndi Mulungu,*+
Munthuyo sangathe kuyankha funso ndi limodzi lomwe pamafunso ake 1,000.
4 Iye ali ndi mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri.+
Ndani angatsutsane naye koma osavulala?+
5 Iye amasuntha* mapiri popanda aliyense kudziwa.
Amawagubuduza atakwiya.
6 Amagwedeza dziko lapansi nʼkulisuntha pamalo ake,
Moti zipilala zake zimagwedera.+
7 Amalamula dzuwa kuti lisawale
Ndipo amaphimba kuwala kwa nyenyezi.+
8 Iye amatambasula kumwamba yekha,+
Ndipo amayenda pamafunde ataliatali a mʼnyanja.+
9 Anapanga gulu la nyenyezi la Asi, la Kesili ndi la Kima,+
Komanso gulu la nyenyezi za kumʼmwera.
10 Amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,+
Zinthu zodabwitsa zimene ndi zosatheka kuziwerenga.+
11 Iye amadutsa pafupi ndi ine koma sinditha kumuona,
Amandidutsa koma ine osamuzindikira.
12 Iye akalanda chinthu, ndani angalimbane naye?
Ndani angamufunse kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
14 Nʼchifukwa chake ndikamamuyankha,
Ndiyenera kusankha bwino mawu anga.
15 Ngakhale nditakhala kuti ndikunena zoona, sindingamuyankhe.+
Koma ndingachonderere woweruza wanga kuti andichitire chifundo.
16 Kodi nditamuitana, angandiyankhe?
Sindikukhulupirira kuti angandimvetsere.
17 Chifukwa iye wandivulaza ndi mavuto angati mphepo yamkuntho,
Ndipo wachulukitsa mabala anga popanda chifukwa.+
18 Sakulola kuti ndikokeko mpweya,
Ndipo akungopitiriza kuwonjezera mavuto anga.
19 Pa nkhani yokhala ndi mphamvu, iye ndi wamphamvu kwambiri.+
Pa nkhani yochita zinthu mwachilungamo, iye amanena kuti: ‘Ndi ndani angandiimbe mlandu?’*
20 Ngakhale ndikanapezeka kuti ndine wosalakwa, pakamwa panga pakanandiweruza kuti ndine wolakwa.
Ngakhale nditakhala wokhulupirika,* adzandipezabe ndi mlandu.*
21 Ngakhale nditakhala wokhulupirika,* sindikudziwa zimene zingandichitikire,
Moyo wangawu sindikuufunanso.*
22 Zonsezi mfundo yake ndi imodzi. Nʼchifukwa chake ndikunena kuti,
‘Iye amawononga onse, osalakwa* komanso oipa.’
23 Anthu atafa mwadzidzidzi ndi madzi osefukira,
Iye angaseke anthu osalakwa akuvutika.
Ngati si iyeyo, ndiye ndi ndani?
25 Panopa masiku anga akufulumira kwambiri kuposa munthu wothamanga.+
Iwo akuthawa asanaone zabwino.
26 Amayenda mofulumira ngati ngalawa za bango,
Ngati ziwombankhanga zimene zimambwandira nyama yoti zidye.
27 Ngati nditanena kuti, ‘Ndiiwala kudandaula kwanga,
Ndisintha maonekedwe a nkhope yanga nʼkukhala wosangalala,’
28 Ndingachitebe mantha chifukwa cha zopweteka zanga zonse,+
Ndipo ndikudziwa kuti simungandipeze kuti ndine wosalakwa.
29 Ndingapezekebe kuti ndine wolakwa.*
Ndiye ndivutikirenji pachabe?+
30 Nditati ndisambe mʼmadzi oyera,*
Komanso kusamba mʼmanja ndi sopo,+
31 Inuyo mungandiviike mʼdzenje la matope,
Moti ngakhale zovala zanga zomwe zinganyansidwe nane.
32 Chifukwa iye si munthu ngati ine kuti ndingamuyankhe,
Kapena kuti titengerane kukhoti.+
34 Ngati iye akanasiya kundimenya,*
Komanso kundiopseza ndi zinthu zake zochititsa mantha,+
35 Ndikanalankhula naye mopanda mantha,
Chifukwa ine sindiopa kulankhula.”
10 “Moyo wanga ndikunyansidwa nawo.+
Ndinena madandaulo anga mwamphamvu.
Ndilankhula mopwetekedwa mtima.*
2 Ndimuuza Mulungu kuti: ‘Musanene kuti ndine wolakwa.
Ndiuzeni chifukwa chake mukulimbana nane.
3 Kodi mukupindula chilichonse mukamandizunza,
Mukamanyoza ntchito ya manja anu,+
Pamene mukugwirizana ndi zolinga za oipa?
4 Kodi maso anu ali ngati a munthu,
Kapena kodi mumaona ngati mmene munthu amaonera?
5 Kodi masiku anu ali ngati masiku a anthu,
Kapena kodi zaka zanu zili ngati za munthu,+
6 Kuti muzifufuza zolakwa zanga
Komanso kuti muzifunafuna tchimo langa?+
8 Manja anu ndi amene anandiumba ndiponso kundipanga,+
Koma tsopano mukufuna kundiwonongeratu.
10 Kodi simunandikhuthule ngati mkaka
Nʼkundichititsa kuti ndiundane ngati tchizi?*
11 Munandiveka khungu ndiponso mnofu,
Ndipo munandiluka ndi mafupa komanso mitsempha.+
12 Mwandipatsa moyo komanso mwandisonyeza chikondi chokhulupirika,
13 Koma inu mukufuna kuchita zinthu zimenezi mwachinsinsi.*
Ndikudziwa kuti zimenezi zachokera kwa inu.
14 Ndikanachimwa mukanandiona,+
Ndipo simukanandikhululukira zolakwa zanga.
15 Ngati ndili wolakwa, tsoka kwa ine!
Ndipo ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingadzutse mutu wanga,+
Chifukwa ndili ndi manyazi kwambiri ndipo ndikuvutika.+
16 Ndikakweza mutu wanga, mumandisaka ngati mmene umachitira mkango+
Ndipo mumasonyezanso mphamvu zanu polimbana nane.
17 Mumabweretsa mboni zatsopano kuti zinditsutse
Ndipo mumawonjezera mkwiyo wanu pa ine,
Moti mavuto anga akungotsatizanatsatizana.
18 Ndiye nʼchifukwa chiyani munanditulutsa mʼmimba mwa mayi anga?+
Zikanakhala bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione.
19 Zikanakhala ngati sindinakhaleko.
Ndikanangochokera mʼmimba nʼkupita kumanda.’
20 Kodi si paja masiku a moyo wanga atsala ochepa?+ Iye andisiye,
Asiye kundiyangʼanitsitsa kuti ndipumuleko pangʼono*+
21 Ndisanapite kumalo amene sindidzabwerako,+
Kudziko lamdima wandiweyani,*+
22 Kudziko lamdima waukulu,
Dziko lamdima wandiweyani komanso lachisokonezo,
Kumene ngakhale kuwala kumafanana ndi mdima.”
11 Zofari+ wa ku Naama anayankha kuti:
2 “Kodi ukuganiza kuti mawu ako onsewa angakhale osayankhidwa?
Kapena kodi kulankhula kwambiri kungachititse kuti munthu akhale wosalakwa?*
3 Kodi zolankhula zako zopanda pake zingachititse kuti anthu akhale chete?
Kodi sipapezeka wokudzudzula chifukwa cha mawu ako onyoza?+
4 Chifukwa ukunena kuti, ‘Zimene ndimaphunzitsa ndi zoyera,+
Ndipo Mulungu amandiona kuti ndine woyera.’+
5 Koma zikanakhala bwino Mulungu akanalankhula yekha
Nʼkukutsegulira pakamwa pake.+
6 Bwenzi atakuululira chinsinsi cha nzeru,
Chifukwa pali zambiri zofunika kuziphunzira zokhudza nzeru yeniyeni.
Bwenzi utazindikira kuti Mulungu walola kuti zolakwa zako zina ziiwalike.
7 Kodi ungazindikire zinthu zozama za Mulungu,
Kapena kodi ungadziwe chilichonse chokhudza* Wamphamvuyonse?
8 Zili kutali kuposa kumwamba. Iwe sungathe kuzipeza.
Nʼzozama kuposa Manda.* Ungadziwe chiyani iwe?
9 Nʼzazitali kuposa dziko lapansi
Ndipo nʼzazikulu kuposa nyanja.
10 Iye akadutsa nʼkugwira winawake nʼkumupititsa kukhoti,
Ndi ndani angatsutsane naye?
11 Iye amadziwa anthu akamachita zachinyengo.
Akaona anthu akuchita zoipa, kodi iye sizimamukhudza?
12 Koma munthu wopanda nzeru angamvetse
Pokhapokha ngati bulu wamʼtchire atabereka munthu.
13 Zikanakhala bwino ukanakonza mtima wako
Nʼkutambasula manja ako kwa iye.
14 Ngati ukuchita chinachake cholakwika, usiyiretu kuchichita,
Ndipo usalole kuti mʼmatenti ako mukhale zinthu zopanda chilungamo.
15 Ukatero, udzadzutsa nkhope yako osachita manyazi,
Udzakhala wolimba ndipo sudzaopa chilichonse.
16 Ukatero udzaiwala mavuto ako,
Udzawaiwala ngati madzi amene adutsa pafupi ndi iwe.
17 Masiku a moyo wako adzakhala owala kuposa masana,
Ngakhale usiku udzakhala ngati mʼmawa.
18 Udzalimba mtima chifukwa chakuti pali chiyembekezo.
Udzayangʼana paliponse ndipo udzagona mopanda mantha.
19 Udzagona popanda aliyense wokuopseza,
Ndipo anthu ambiri adzafuna kuti uwachitire chifundo.
20 Koma maso a anthu oipa sadzaonanso,
Ndipo sadzapeza malo othawirako,
12 Kenako Yobu anayankha kuti:
2 “Zoonadi, anthu inu mukudziwa zinthu zambiri,*
Ndipo nzeru zidzathera limodzi ndi inu.
3 Koma inenso ndine wozindikira* ngati inuyo.
Si ine munthu wamba poyerekezera ndi inu.
Ndi ndani amene sakudziwa zimenezi?
4 Ine ndakhala chinthu choseketsa kwa anzanga,+
Ndakhala munthu amene akuitana Mulungu kuti amuyankhe.+
Munthu wolungama komanso wosalakwa wakhala choseketsa.
5 Amene zinthu zikuwayendera bwino amanyoza amene akumana ndi tsoka,
Iwo amaganiza kuti limagwera anthu okhawo amene akukumana kale ndi mavuto.*
6 Anthu akuba amakhala mwamtendere mʼmatenti awo,+
Amene amakwiyitsa Mulungu amakhala otetezeka,+
Anthu amene mulungu wawo ali mʼmanja mwawo.
7 Koma funsa nyama ndipo zidzakuphunzitsa.
Komanso mbalame zamumlengalenga, ndipo zidzakuuza.
8 Kapena chita chidwi* ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa,
Komanso nsomba zamʼnyanja ndipo zidzakuuza.
9 Kodi ndi ndani pa zonsezi amene sakudziwa
Kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi?
12 Kodi si paja okalamba amakhala ndi nzeru,+
Ndipo amene akhala moyo wautali si paja amamvetsa zinthu?
13 Mulungu ali ndi nzeru komanso mphamvu.+
Iye amamvetsa zinthu ndipo adzakwaniritsa cholinga chake.+
14 Iye akagwetsa chinthu, sichingamangidwenso,+
Zimene iye watseka, palibe munthu amene angatsegule.
16 Iye ali ndi mphamvu komanso nzeru zopindulitsa.+
Ali ndi mphamvu pa munthu amene akusochera ndi amene akusocheretsa ena.
17 Iye amachititsa kuti alangizi ayende opanda nsapato,*
Ndipo amapusitsa oweruza.+
18 Amamasula zingwe zimene mafumu amangira anthu,+
Ndipo amawamanga lamba mʼchiuno mwawo.
19 Amachititsa kuti ansembe ayende opanda nsapato,+
Ndipo amachotsa paudindo olamulira amphamvu.+
20 Alangizi okhulupirika amawasowetsa chonena,
Ndipo amachotsa kuzindikira kwa amuna achikulire,*
21 Iye amachititsa manyazi anthu olemekezeka,+
Ndipo amachititsa anthu amphamvu kuti akhale ofooka.*
22 Amaulula zinthu zozama zimene zili mumdima,+
Ndipo amabweretsa kuwala mumdima wandiweyani.
23 Amachititsa mitundu kuti ikhale yamphamvu nʼcholinga choti aiwononge.
Amakulitsa mitundu kuti aipititse ku ukapolo.
24 Amachotsa nzeru za atsogoleri* a anthuwo,
Ndipo amawachititsa kuti azingoyendayenda mʼchipululu mmene mulibe njira.+
25 Iwo amafufuza mumdima+ mmene mulibe kuwala,
Iye amawachititsa kuti aziyendayenda ngati anthu oledzera.”+
13 “Inde, maso anga aona zonsezi,
Khutu langa lamva komanso lazimvetsa.
2 Zimene inu mukuzidziwa, inenso ndikuzidziwa.
Si ine munthu wamba poyerekezera ndi inu.
3 Ine ndikanakonda kulankhula ndi Wamphamvuyonse,
Ndikulakalaka nditalankhula ndi Mulungu zokhudza mlandu wangawu.+
4 Koma inu mukundinamizira mabodza.
Nonsenu ndinu madokotala osathandiza.+
5 Zikanakhala bwino mukanangokhala chete,
Zimenezi zikanasonyeza kuti ndinu anzeru.+
6 Mvetserani mfundo zanga,
Ndipo tcherani khutu pamene ndikufotokoza mlandu wanga.
7 Kodi mukulankhula zopanda chilungamo mʼmalo mwa Mulungu?
Ndipo kodi mukulankhula zachinyengo mʼmalo mwa iye?
8 Kodi mukhala kumbali yake?*
Kodi mungakhale kumbali ya Mulungu woona pamlandu wake?
9 Kodi zingakuyendereni bwino ngati atakufufuzani?+
Kodi mungamupusitse ngati mmene mungapusitsire munthu?
10 Iye adzakudzudzulani ndithu,
Mukadzayesa kuchita mwachinsinsi zinthu zokondera.+
11 Kodi kulemekezeka kwake sikudzakuchititsani mantha?
Ndipo kodi sadzakuchititsani kuti mumuope?
12 Mawu anu anzeru* nʼchimodzimodzi ndi miyambi yosathandiza ngati phulusa.
Mawu anu odziteteza ndi osathandiza ngati zishango zadothi.
13 Khalani chete pamaso panga, kuti ineyo ndilankhule.
Kenako chilichonse chimene chingabwere kwa ine, chibwere.
14 Nʼchifukwa chiyani ndikuika moyo wanga pachiswe,*
Komanso kunyamula moyo wanga mʼmanja?
15 Ngakhale Mulungu atandipha, ndipitirizabe kumukhulupirira,+
Ndisonyeza pamaso pake kuti ndine wosalakwa.*
17 Mvetserani mawu anga mosamala,
Mvetserani mwatcheru zimene ndikunena.
18 Onani, tsopano ndakonzeka kubweretsa mlandu wanga kuti uweruzidwe.
Ine ndikudziwa kuti sindinalakwe.
19 Ndi ndani amene angatsutsane nane?
Ngati nditapanda kulankhula, ndikhoza kufa.*
20 Inu Mulungu, mundichitire zinthu ziwiri zokha,*
Kuti ndisabisale pamaso panu:
21 Chotsani dzanja lanu lolemera nʼkuliika kutali kwambiri ndi ine,
Ndipo musapitirize kundiopseza.+
22 Muitane ndipo ine ndivomera,
Kapena ndilankhule ndipo inu mundiyankhe.
23 Kodi ndinalakwa chiyani, nanga machimo anga ndi ati?
Ndiuzeni zimene ndinalakwa komanso tchimo langa.
25 Kodi mukufuna kuopseza tsamba louluzika ndi mphepo
Kapena kuthamangitsa udzu wouma?
26 Inu mukupitiriza kulemba milandu yoopsa yokhudza ine,
Ndipo mukundilanga chifukwa cha machimo amene ndinachita ndili mnyamata.
27 Mwaika mapazi anga mʼmatangadza,
Mumayangʼanitsitsa njira zanga zonse,
Ndipo mumatsatira paliponse pamene phazi langa laponda.
28 Choncho munthu* amaola ngati chinthu chimene chayamba kuwonongeka,
Ngati chovala chimene chadyedwa ndi njenjete.”*
4 Kodi munthu wochimwa angabereke munthu wosachimwa?*+
Ayi nʼzosatheka.
5 Masiku a munthu ndi odziwika,
Ndipo chiwerengero cha miyezi yake chili mʼmanja mwanu.
Mwamuikira malire kuti asapitirire.+
6 Siyani kumuyangʼanitsitsa kuti apume,
Mpaka atamaliza tsiku lake ngati mmene amachitira waganyu.+
7 Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo.
Ukadulidwa umaphukanso,
Ndipo nthambi zake zidzapitiriza kukula.
8 Ngati muzu wake wakalamba mʼnthaka,
Ndipo chitsa chake chafa mʼdothi,
9 Ukadzangomva fungo la madzi udzaphukira,
Ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo watsopano.
10 Koma munthu amafa ndipo mphamvu zake zonse zimatha.
Munthu akafa, kodi amapita kuti?+
11 Madzi amatha mʼnyanja,
Ndipo mtsinje umaphwa nʼkuuma.
12 Munthu nayenso amagona pansi ndipo sadzuka.+
Sadzadzuka mpaka kumwamba kutachoka,
Sadzadzutsidwa ku tulo take.+
13 Zikanakhala bwino mukanandibisa mʼManda,*+
Mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utadutsa,
Zikanakhala bwino mukanandiikira nthawi nʼkudzandikumbukira.+
14 Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?+
Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza,
Mpaka mpumulo wanga utafika.+
15 Inu mudzaitana ndipo ine ndidzakuyankhani.+
Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.
16 Koma panopa mukungokhalira kuwerenga paliponse pamene mapazi anga aponda,
Mukungoyangʼana machimo anga basi.
17 Kulakwa kwanga mwakutsekera mʼthumba,
Ndipo mwamata machimo anga ndi zomatira.
18 Phiri limagwa nʼkugumukagumuka,
Ndipo thanthwe limasuntha pamalo ake.
19 Madzi amaperepesa miyala
Ndipo mitsinje yake imakokolola dothi lapadziko lapansi.
Inunso mwawononga chiyembekezo cha munthu.
20 Mukupitiriza kumugonjetsa mpaka atatheratu.+
Mwasintha maonekedwe ake nʼkumuthamangitsa.
21 Ana ake amalemekezedwa, koma iye sadziwa zimenezo.
Iwo amakhala onyozeka, koma iye sazindikira zimenezo.+
22 Amamva kuwawa pa nthawi yokhayo imene ali ndi moyo,
Iye amalira pa nthawi yokhayo imene ali moyo.”
15 Elifazi+ wa ku Temani anayankha kuti:
2 “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu opanda pake,*
Kapena angadzaze mimba yake ndi mphepo yakumʼmawa?
3 Kungodzudzula ndi mawu okha nʼkopanda ntchito,
Ndipo kulankhula kokha nʼkosathandiza.
4 Chifukwa iweyo ukupangitsa kuti anthu asamaope kwambiri Mulungu,
Ndipo ukupangitsa kuti asamaganizire mozama za Mulungu.
5 Zolakwa zako nʼzimene zikukupangitsa kuti uzilankhula choncho,*
Ndipo wasankha kulankhula mwa ukathyali.
6 Pakamwa pako mʼpamene pakusonyeza kuti ndiwe wolakwa, osati ine,
Ndipo milomo yako ikukutsutsa.+
7 Kodi munthu woyambirira kubadwa unali iwe?
Kapena kodi unabadwa mapiri asanakhaleko?
8 Kodi umamvetsera nkhani zachinsinsi za Mulungu?
Kapena kodi umaona kuti wanzeru ndiwe wekha?
9 Ukudziwa chiyani chimene ife sitikudziwa?+
Ndipo nʼchiyani chimene umamvetsa chimene ifeyo sitingachimvetse?
10 Pakati pathu pali aimvi ndi okalamba,+
Amuna omwe ndi achikulire kuposa bambo ako.
11 Kodi mawu otonthoza ochokera kwa Mulungu sakukukwanira?
Kapena kodi kulankhula nawe mawu odekha sikunakukwanire?
12 Nʼchifukwa chiyani mtima wako ukudzikweza?
Ndipo nʼchifukwa chiyani ukutiyangʼana mokwiya?
13 Chifukwa wakwiyira Mulungu,
Nʼchifukwa chake ukulankhula mwa njira imeneyi.
14 Kodi munthu ndi ndani kuti akhale woyera?
Kapena aliyense wobadwa kwa mkazi kuti akhale wolungama?+
15 Iyetu sakhulupirira angelo ake,
Ndipo ngakhale kumwamba si koyera mʼmaso mwake.+
16 Nanga angakhulupirire bwanji munthu wonyansa amene amachita zoipa zokhazokha,+
Munthu yemwe amamwa zinthu zopanda chilungamo ngati madzi?
17 Ine ndikuuza ndipo undimvetsere!
Ndikufotokozera zimene ndaona,
18 Zimene anthu anzeru amanena,
Zinthu zimene anamva kuchokera kwa makolo awo ndipo sanazibise.+
19 Dziko linaperekedwa kwa iwowo basi,
Ndipo palibe mlendo amene anadutsa pakati pawo.
20 Munthu woipa amazunzidwa masiku onse a moyo wake,
Pa zaka zonse zimene zinasungidwira wolamulira wankhanza.
21 Amamva phokoso lochititsa mantha mʼmakutu ake,+
Pa nthawi yamtendere achifwamba amamuukira.
22 Iye sakhulupirira kuti adzatuluka mumdima,+
Ndipo akudikira kuti aphedwe ndi lupanga.
23 Amayendayenda pofunafuna chakudya ndipo amafunsa kuti: ‘Kodi chili kuti?’
Iye akudziwa bwino kuti tsiku lamdima layandikira.
24 Chisoni komanso mavuto zikungokhalira kumuchititsa mantha.
Zipitiriza kumuchititsa mantha ngati mfumu yamphamvu imene yakonzekera kuyambitsa nkhondo.
25 Chifukwa amakweza dzanja lake kuti atsutsane ndi Mulungu,
Ndipo amafuna kusonyeza kuti ndi wamphamvu kuposa Wamphamvuyonse.
26 Iye amalimbana ndi Mulungu mwamakani,
Atatenga chishango chake cholimba komanso chochindikala.
27 Nkhope yake yanenepa,
Ndipo mimba yake yakula chifukwa chonenepa.*
28 Iye amakhala mʼmizinda imene idzawonongedwe,
Mʼnyumba zimene simudzakhala aliyense,
Zimene zidzakhale milu ya miyala.
29 Iye sadzalemera ndipo chuma chake sichidzachuluka.
Zinthu zake sizidzafalikira padziko.
30 Iye sangathe kuthawa mdima,
Moto udzaumitsa nthambi yake,*
Ndipo adzaphedwa ndi mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu.+
31 Iye asasochere nʼkukhulupirira zinthu zopanda pake,
Chifukwa zimene adzapeze zidzakhala zopanda pake.
32 Zimenezi zimuchitikira posachedwapa,
Ndipo nthambi zake sizidzakula mosangalala.+
33 Iye adzakhala ngati mtengo wa mpesa umene mphesa zake zimagwa zisanapse,
Komanso ngati mtengo wa maolivi umene umayoyola maluwa ake.
34 Chifukwa msonkhano wa anthu oipa* ndi wopanda phindu,+
Ndipo moto udzanyeketsa matenti a anthu aziphuphu.
35 Iwo amatenga pakati pamavuto nʼkubereka zinthu zoipa,
Ndipo mimba yawo imatulusa zachinyengo.”
16 Yobu anayankha kuti:
2 “Ndamvapo zinthu zambiri ngati zimenezi.
Nonsenu ndinu otonthoza obweretsa mavuto!+
3 Kodi simusiya kulankhula mawu opanda pakewa?*
Chikukupwetekani nʼchiyani kuti muziyankha chonchi?
4 Inenso ndikanatha kulankhula ngati mmene mukuchitiramu.
Mukanakhala kuti mukukumana ndi mavuto ngati angawa,*
Ndikanalankhula mawu ambiri okudzudzulani
Komanso kukupukusirani mutu.+
5 Koma sindikanatero, mʼmalomwake ndikanakulimbikitsani ndi mawu amʼkamwa mwanga,
Ndipo mawu otonthoza apakamwa panga akanakulimbikitsani.+
6 Ndikalankhula, ululu wanga sukuchepa,+
Ndipo ndikasiya kulankhula, ululu wanga sukutha.
8 Komanso iye wandigwira ndipo anthu ena akuona zimenezi,
Moti kuwonda kwangaku ndi umboni wonditsutsa.
9 Mkwiyo wa Mulungu wandikhadzula ndipo akundisungira chidani.+
Iye akundikukutira mano.
Mdani wanga akundiyangʼana mokwiya nʼcholinga choti andivulaze.+
10 Anthu atsegula kukamwa kwawo kuti andimeze.+
Ndipo andimenya mbama pofuna kundichititsa manyazi.
Iwo asonkhana ambirimbiri kuti alimbane nane.+
11 Mulungu wandipereka kwa tianyamata,
Ndipo wandiponya mʼmanja mwa oipa.+
12 Ine ndinali pa mtendere koma iye wandiphwanya.+
Wandigwira kumbuyo kwa khosi nʼkundimenyetsa pansi,
Kenako wandiponyera mivi yake.
13 Anthu ake oponya mivi ndi uta andizungulira.+
Iye waboola impso zanga+ ndipo sakumva chisoni,
Wakhuthulira ndulu yanga pansi.
14 Iye akungokhalira kundiboola ngati khoma.
Akundithamangira ngati msilikali.
16 Nkhope yanga yafiira chifukwa cholira,+
Ndipo pazikope zanga pali mdima wandiweyani,*
17 Ngakhale kuti manja anga sanachite zachiwawa,
Ndipo pemphero langa ndi loyera.
18 Iwe dziko lapansi, usabise magazi anga.+
Alole kuti alire mʼmalo mwa ine.
19 Ngakhale panopa, mboni yanga ili kumwamba,
Amene angandichitire umboni ali mʼmwamba.
21 Wina aweruze pakati pa munthu ndi Mulungu,
Ngati mmene angaweruzire pakati pa munthu ndi mnzake.+
22 Chifukwa ndangotsala ndi zaka zochepa,
Ndipo ndidzayenda mʼnjira imene sindidzabwereranso.”+
17 “Mzimu wanga wasweka, masiku anga atha.
Kumanda kukundidikirira.+
2 Anthu onyoza andizungulira,+
Ndipo diso langa likuyenera kuyangʼanitsitsa* khalidwe lawo lopanduka.
3 Chonde, landilani chikole changa ndipo muchisunge.
Kodi pali winanso amene angagwirane nane chanza nʼkulonjeza kuti andithandiza?+
4 Mwawapangitsa kuti akhale osazindikira,+
Nʼchifukwa chake simunawalemekeze.
5 Anthu amenewa amauza anzawo kuti agawana nawo chuma chawo,
Pamene ana awo akulephera kuona bwinobwino chifukwa cha njala.
7 Chifukwa cha kuzunzika, maso anga ayamba kuchita mdima.+
Manja ndi miyendo yanga zakhala ngati mthunzi.
8 Anthu owongoka mtima akuyangʼana zimenezi modabwa,
Ndipo munthu wosalakwa wakhumudwa chifukwa cha anthu oipa.*
9 Wolungama akuyendabe panjira yake,+
Ndipo amene ali ndi manja oyera, mphamvu zake zikuwonjezereka.+
10 Komabe, nonsenu mungathe kubwera nʼkuyambiranso kundinena,
Chifukwa sindikuonapo aliyense wanzeru pakati panu.+
12 Anzanga akumasintha usiku kuti ukhale masana.
Iwo akunena kuti, ‘Chifukwa choti kuli mdima, kuwala kuyenera kuti kwayandikira.’
14 Ndidzaitana dzenje*+ kuti, ‘Ndinu bambo anga!’
Kwa mphutsi ndidzati, ‘Mayi anga ndi mlongo wanga!’
15 Ndiye chiyembekezo changa chili kuti?+
Kodi pali amene akuona kuti ndili ndi chiyembekezo?
16 Chidzapita* ku Manda* otsekedwa ndi zitsulo,
Pa nthawi imene tonsefe tidzapitira limodzi kufumbi.”+
18 Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:
2 “Kodi usiya nthawi yanji kulankhula choncho?
Sonyeza kuti ndiwe wozindikira kuti nafenso tilankhule.
4 Ngakhale utadzikhadzulakhadzula chifukwa choti wakwiya,
Kodi dziko lapansi lingasiyidwe chifukwa cha iwe?
Kapena kodi thanthwe lingasunthe pamalo ake?
5 Inde, kuwala kwa woipa kudzazimitsidwa,
Ndipo malawi a moto wake sadzawala.+
6 Kuwala kwa mutenti yake kudzazima,
Ndipo nyale imene ili mutenti yake idzazimitsidwa.
7 Adzakhala alibe mphamvu zoti nʼkuyendera,
Ndipo mapulani ake adzamubweretsera mavuto.+
8 Mapazi ake adzamugwetsera mu ukonde,
Ndipo adzayenda mʼzingwe za ukondewo.
9 Msampha udzamugwira chidendene.
Khwekhwe lidzamukola.+
10 Chingwe chabisidwa pansi kuti chimukole,
Ndipo msampha uli panjira yake.
11 Zoopsa zimamuchititsa mantha paliponse,+
Ndipo zimamuthamangitsa zili naye pafupi kwambiri.
13 Khungu lake ladyeka.
Matenda oopsa kwambiri agwira* manja ndi miyendo yake.
14 Iye adzachotsedwa mʼmalo otetezeka amutenti yake,+
Ndipo adzamupititsa kwa mfumu ya zinthu zoopsa.*
16 Pansi, mizu yake idzauma,
Ndipo pamwamba, nthambi zake zidzafota.
17 Anthu sadzamukumbukiranso padziko lapansi,
Ndipo mumsewu dzina lake silidzadziwika.*
18 Adzamuchotsa powala nʼkumupititsa kumdima
Ndipo adzamuthamangitsa padziko lapansi.
19 Iye sadzasiya ana kapena mbadwa pakati pa anthu ake,
Ndipo sipadzakhala wopulumuka pamalo amene iye akukhala.*
20 Tsiku la tsoka lake likadzafika, anthu a Kumadzulo adzachita mantha kwambiri,
Ndipo anthu a Kumʼmawa adzagwidwa ndi mantha aakulu.
21 Izi nʼzimene zimachitikira matenti a munthu wochita zoipa,
Komanso malo a munthu amene sadziwa Mulungu.”
19 Yobu anayankha kuti:
4 Ngati ndalakwitsadi chinachake,
Zotsatira zake ndithana nazo ndekha.
5 Ngati mukupitiriza kudzikweza pamaso panga,
Nʼkumanena kuti ndikuyenera kukumana ndi mavuto amene ndikukumana nawowa,
6 Dziwani kuti ndi Mulungu amene wandisocheretsa,
Ndipo wandikola ndi ukonde wake wosakira nyama.
7 Ine ndakhala ndikulira chifukwa cha mavuto anga, koma palibe amene akundichitira zabwino.+
Ndakhala ndikufuula popempha thandizo, koma chilungamo sichikupezeka.+
8 Iye watseka njira yanga ndi khoma lamiyala moti sindingathe kudutsa,
Watchinga njira zanga ndi mdima.+
9 Iye wandichotsera ulemerero wanga,
Ndipo wandivula chisoti chaulemu kumutu kwanga.
10 Wandigumula mbali zonse mpaka ndatheratu.
Chiyembekezo changa wachizula ngati mtengo.
11 Mkwiyo wake wandiyakira,
Ndipo akungondiona ngati mdani wake.+
12 Asilikali ake asonkhana pamodzi nʼkundizungulira,
Ndipo amanga misasa yawo kuzungulira tenti yanga.
13 Abale anga enieni wawathamangitsira kutali ndi ine,
Ndipo anthu amene akundidziwa akundisala.+
15 Alendo amʼnyumba mwanga+ komanso akapolo anga aakazi akundiona ngati munthu wachilendo.
Ndine mlendo kwa iwo.
16 Ndaitana wantchito wanga koma sakundiyankha.
Ndamuchonderera ndi pakamwa panga kuti andichitire chifundo.
18 Ngakhale ana angʼonoangʼono akundinyoza.
Ndikaimirira, akumayamba kundinyogodola.
21 Ndichitireni chifundo anzanganu, ndichitireni chifundo,
Chifukwa dzanja la Mulungu landikhudza.+
22 Nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kundizunza ngati mmene Mulungu akuchitira?+
23 Zikanakhala bwino mawu anga akanalembedwa,
Zikanakhala bwino akanalembedwa mʼbuku!
24 Akanalembedwa pathanthwe mochita kugoba kuti akhale mpaka kalekale
Akanalembedwa ndi chitsulo chogobera nʼkuthirapo mtovu.
25 Ine ndikudziwa bwino kuti wondiwombola+ ali moyo,
Iye adzabwera nthawi ina ndipo adzaimirira padziko lapansi.*
26 Pambuyo poti khungu langa lawonongedwa chonchi,
Ndidakali moyo, ndidzaona Mulungu,
27 Ine ndidzamuona ndekha,
Maso angawa adzamuona, osati a munthu wina.+
Koma mkati mwanga ndikumva kupanikizika kwambiri.*
28 Chifukwa inu mukunena kuti, ‘Tikukuzunza mwa njira yanji?’+
Popeza amene ndayambitsa mavutowa ndine.
29 Mukuyenera kuopa lupanga,+
Chifukwa mukalakwitsa zinthu, mudzalangidwa ndi lupanga,
Mukuyenera kudziwa kuti kuli woweruza.”+
20 Zofari+ wa ku Naama anayankha kuti:
2 “Maganizo anga akundivutitsa ndipo achititsa kuti ndiyankhe
Chifukwa mumtima mwanga muli mkwiyo.
3 Ndamva zimene wanena pondinyoza,
Ndipo ndikuyankha chifukwa ndine womvetsa zinthu.*
4 Uyenera kuti wakhala ukudziwa zimenezi,
Chifukwa zakhala zili choncho kuchokera pamene munthu* anaikidwa padziko lapansi,+
5 Kuti kufuula kwa chisangalalo kwa munthu woipa sikukhalitsa,
Ndiponso kuti kusangalala kwa woipa* kumakhala kwa kanthawi.+
6 Ngakhale kuti ulemerero wake umafika kumwamba,
Ndipo mutu wake umafika mʼmitambo,
7 Adzatheratu mofanana ndi ndowe zake.
Anthu amene ankamuona adzati, ‘Kodi munthu uja ali kuti?’
8 Iye adzauluka ngati maloto ndipo sadzamupeza.
Adzathamangitsidwa ngati masomphenya a usiku.
9 Diso limene linamuona silidzamuonanso,
Ndipo malo ake sadzamuonanso.+
10 Ana ake adzapempha anthu osauka kuti awathandize,
Ndipo iye adzabweza chuma chimene analanda kwa anthu ena.+
12 Ngati zoipa zimatsekemera mʼkamwa mwake,
Ngati amazibisa pansi pa lilime lake,
13 Ngati amazisunga ndipo safuna kuzilavula,
Koma amapitiriza kuzivumata mʼkamwa mwake,
14 Chakudya chake chidzasasa mʼmatumbo mwake.
Chidzakhala ngati poizoni wa mamba* mʼthupi mwake.
15 Wameza chuma, koma adzachisanza.
Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwake.
16 Adzayamwa poizoni wa mamba,
Mano a mphiri adzamupha.*
17 Sadzaona ngalande za madzi,
Mitsinje yosefukira ndi uchi komanso mafuta amumkaka.
19 Chifukwa waphwanya osauka nʼkuwasiya,
Walanda nyumba imene sanamange.
20 Koma sadzapeza mtendere mumtima mwake.
Chuma chake sichidzamupulumutsa.
21 Palibe chimene chatsala choti alande,
Nʼchifukwa chake zinthu sizidzapitiriza kumuyendera bwino.
22 Chuma chake chikadzafika pachimake, adzakhala ndi nkhawa,
Tsoka lalikulu lidzamugwera.
23 Pamene akudzazitsa mimba yake,
Mulungu adzamutumizira mkwiyo wake woyaka moto,
Adzauvumbitsa pa iye mpaka udzafika mʼmatumbo mwake.
24 Akamadzathawa zida zachitsulo,
Mivi yoponyedwa ndi uta wakopa idzamulasa.
26 Chuma chake chidzasowa mumdima wandiweyani.
Moto umene palibe amene waukupizira udzamupsereza.
Munthu amene adzapulumuke mutenti yake adzakumana ndi tsoka.
27 Kumwamba kudzaulula zolakwa zake,
Ndipo dziko lapansi lidzamuukira.
28 Madzi osefukira adzakokolola nyumba yake.
Adzakhala mtsinje wamphamvu pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu.
29 Ili ndi gawo la munthu woipa lochokera kwa Mulungu,
Cholowa chimene Mulungu walamula kuti alandire.”
21 Yobu anayankha kuti:
2 “Mvetserani mwatcheru zimene ndikufuna kunena.
Mukachita zimenezi ndiye kuti munditonthoza.
3 Ndilezereni mtima pamene ndikulankhula.
Ndikamaliza kulankhula, mukhoza kuyamba kundinyoza.+
4 Kodi madandaulo anga akupita kwa munthu?
Zikanakhala choncho, kodi ndikanakhalabe woleza mtima?*
5 Tandiyangʼaneni ndipo mudabwa,
Gwirani pakamwa panu.
6 Ndikaziganizira, zikumandisokoneza,
Ndipo thupi langa lonse likumanjenjemera.
8 Ana awo amakhala nawo limodzi nthawi zonse,
Ndipo amakhala ndi moyo wautali moti amaona zidzukulu zawo.
9 Nyumba zawo nʼzotetezeka ndipo saopa chilichonse,+
Mulungu sawalanga ndi ndodo yake.
10 Ngʼombe zawo zamphongo sizilephera kupereka bere.
Ngʼombe zawo zazikazi zimabereka ndipo sizibereka ana akufa.
11 Anyamata awo amathamangira panja ngati nkhosa,
Ndipo ana awo amadumphadumpha.
12 Iwo amaimba pogwiritsa ntchito maseche ndi azeze.
Ndipo amasangalala akamva kulira kwa chitoliro.+
14 Koma iwo amauza Mulungu woona kuti, ‘Tisiyeni!
Sitikufuna kudziwa njira zanu.+
15 Kodi Wamphamvuyonse ndi ndani kuti timutumikire?+
Ndipo kodi tingapindule chiyani ngati titamudziwa?’+
16 Koma ndikudziwa kuti alibe mphamvu zochititsa kuti zinthu ziwayendere bwino pa moyo wawo.+
Zimene anthu oipa amaganiza nʼzosiyana* ndi zimene ndimaganiza.+
17 Kodi nyale ya oipa imazimitsidwa kangati?+
Ndipo tsoka limawagwera kangati?
Kodi Mulungu amawawononga kangati atakwiya?
18 Kodi iwo anayamba akhalapo ngati udzu wouluzika ndi mphepo
Kapena ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo yamkuntho?
19 Mulungu adzalanga ana a munthu woipa chifukwa cha zolakwa za bambo awo.
Koma Mulungu amulangenso iyeyo kuti adziwe kulakwa kwake.+
20 Maso ake aone iye akamawonongedwa,
Ndipo adzamwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.+
21 Ngati chiwerengero cha masiku a moyo wake chitachepa,*
Sadzasamala zimene zidzachitikire anthu amʼnyumba yake iyeyo atapita.+
22 Kodi pali aliyense amene angaphunzitse Mulungu chilichonse,*+
Pamene Mulunguyo ndi amene amaweruza ngakhale anthu apamwamba?+
23 Munthu wina amafa adakali ndi mphamvu+
Ali pa mtendere komanso wopanda nkhawa,+
24 Ntchafu zake zitafufuma ndi mafuta,
Ndipo mafupa ake ali olimba.*
25 Koma munthu winanso amafa ali ndi nkhawa zazikulu,*
Asanalawepo zinthu zabwino.
27 Inetu ndikudziwa bwino zimene mukuganiza,
Ndiponso mapulani amene mukupanga kuti mundichitire zoipa.+
28 Chifukwa mukunena kuti, ‘Kodi nyumba ya munthu wolemekezeka ili kuti,
Nanga tenti imene munthu woipa ankakhala ili kuti?’+
29 Kodi simunafunse anthu apaulendo?
Kodi simunafufuze mosamala zimene amanena,*
30 Zoti munthu woipa amapulumuka pa tsiku la tsoka,
Ndiponso kuti pa tsiku la mkwiyo amapulumutsidwa?
31 Ndi ndani angamuuze pamasomʼpamaso kuti akuyenda njira yoipa,
Ndipo ndi ndani angamubwezere pa zimene wachita?
32 Akadzapita naye kumanda,
Anthu adzachezera pamanda ake.
33 Dothi lamʼchigwa* limene adzamukwirire nalo lidzakhala lotsekemera kwa iye,+
Ndipo anthu onse adzamutsatira*+
Mofanana ndi anthu osawerengeka amene anapita iye asanapite.
34 Ndiye nʼchifukwa chiyani mukunditonthoza ndi mawu osathandiza?+
Ndipo mayankho anu ndi mabodza okhaokha.”
22 Elifazi+ wa ku Temani anayankha kuti:
2 “Kodi munthu angakhale waphindu kwa Mulungu?
Kodi aliyense wozindikira angakhale waphindu kwa iye?+
3 Kodi zoti ndiwe wolungama, Wamphamvuyonse ali nazo ntchito?*
Kapena kodi amapindula chilichonse chifukwa choti umachita zinthu mokhulupirika?+
4 Kodi iye adzakulanga
Nʼkupita nawe kwa woweruza chifukwa choti umaopa Mulungu?
5 Kodi si chifukwa choti ndiwe woipa kwambiri
Ndipo ukupitiriza kuchita zolakwa?+
6 Paja umalanda abale ako chikole popanda chifukwa,
Ndipo anthu umawavula zovala zawo nʼkuwasiya ali maliseche.*+
7 Munthu wotopa sumupatsa madzi akumwa,
Ndipo munthu wanjala umamumana chakudya.+
8 Munthu wamphamvu, dziko ndi lake.+
Ndipo munthu amene wamukondera amakhala mmenemo.
9 Koma akazi amasiye unawabweza chimanjamanja,
Ndipo mikono ya ana amasiye unaiphwanya.
10 Nʼchifukwa chake misampha* yakuzungulira,+
Ndipo umachita mantha ndi zoopsa zadzidzidzi.
11 Nʼchifukwa chake pali mdima waukulu moti sungathe kuona,
Ndipo wamira mʼmadzi osefukira.
12 Kodi Mulungu sali pamwamba kuposa kumwamba?
Ndipo ona kuti nyenyezi zonse zilinso pamwamba kwambiri.
13 Koma iwe wanena kuti: ‘Mulungu akudziwa chiyani?
Kodi angathe kuweruza pali mdima wandiweyani?
14 Mitambo imamutchingira moti sangathe kuona,
Pamene akuyendayenda kumwamba.’
15 Kodi uyenda panjira yakalekale
Imene anthu oipa anayendamo,
16 Anthu amene imfa inawatenga nthawi yawo isanakwane,*
17 Iwo ankauza Mulungu woona kuti: ‘Tisiyeni!
Komanso kuti ‘Kodi Wamphamvuyonse angatichite chiyani?’
18 Chonsecho Mulungu ndi amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino.
(Maganizo oipawa ndi osiyana ndi maganizo anga.)
19 Olungama adzaona anthu amenewa akuwonongedwa ndipo adzasangalala,
Ndipo wosalakwa adzawaseka kuti:
20 ‘Adani athu awonongedwa,
Ndipo moto udzapsereza chilichonse chimene asiya.’
21 Udziwe Mulungu ndipo udzakhala pa mtendere.
Ukatero zinthu zabwino zidzabwera kwa iwe.
22 Landira malangizo ochokera pakamwa pake,
Ndipo usunge mawu ake mumtima mwako.+
23 Ukabwerera kwa Wamphamvuyonse, udzabwezeretsedwa mwakale.+
Ngati utachotsa zosalungama mutenti yako,
24 Ukataya golide wako mʼfumbi,
Ndipo ukataya golide wa ku Ofiri+ mʼzigwa zamiyala,*
25 Wamphamvuyonse adzakhala golide wako,
Ndiponso adzakhala siliva wako wabwino kwambiri.
26 Ukatero udzasangalala kwambiri ndi Wamphamvuyonse,
Ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.
27 Udzamudandaulira ndipo adzakumvetsera.
Udzapereka zimene unalonjeza.
28 Chilichonse chimene ukufuna kuchita chidzakuyendera bwino,
Ndipo kuwala kudzaunikira njira yako.
29 Ukamalankhula modzitukumula udzachititsidwa manyazi,
Koma wodzichepetsa* adzamupulumutsa.
30 Iye adzapulumutsa anthu osalakwa.
Choncho ngati manja ako ali oyera, udzapulumutsidwa ndithu.”
23 Yobu anayankha kuti:
3 Ndikanadziwa kumene ndingapeze Mulungu,+
Ndikanapita kumalo kumene iye amakhala.+
4 Bwenzi nditapititsa mlandu wanga kwa iye
Ndipo ndikanafotokoza mfundo zodziikira kumbuyo.
5 Ndikanamvetsera zimene akanandiyankha,
Ndipo ndikanasunga zimene wandiuza.
6 Kodi akanalimbana nane pogwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu?
Ayi ndithu, iye akanandimvetsera.+
7 Kumeneko, mlandu wa munthu wowongoka mtima udzaweruzidwa pamaso pake,
Ndipo Woweruza wanga adzagamula kuti ndilibe mlandu mpaka kalekale.
8 Koma ndikapita kumʼmawa, iye kulibe.
Ndipo ndikabwerako, sindimupeza.
9 Iye akamagwira ntchito kumanzere, sindingamuyangʼane.
Kenako amatembenukira kumanja, koma sindimuonabe.
10 Koma akudziwa njira imene ine ndikudutsa.+
Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide woyenga bwino.+
11 Mapazi anga akuponda mmene mapazi ake akuponda.
Ndapitiriza kuyenda mʼnjira yake ndipo sindinapatuke.+
12 Sindinasiye kutsatira malamulo otuluka pakamwa pake.
Ndasunga mosamala mawu ake+ kuposa zimene amafuna kuti ndichite.*
13 Akatsimikiza kuti achite zinthu, ndi ndani angamuletse?+
Akafuna kuchita chinthu, amachitadi.+
14 Iye adzachita zonse zimene wakonza kuti andichitire,
Ndipo pali zinthu zambiri zoterezi zimene akuganiza kuti andichitire.
15 Nʼchifukwa chake ndikuda nkhawa ndi zimene Mulungu angandichitire.
Ndikaganizira za iye, ndikumachita mantha kwambiri.
16 Mulungu wachititsa kuti nditaye mtima,
Ndipo Wamphamvuyonse wachititsa kuti ndikhale ndi mantha.
17 Koma mdima sunapangitse kuti ndisiye kulankhula,
Kapenanso mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.”
24 “Nʼchifukwa chiyani Wamphamvuyonse sanakhazikitse nthawi yachiweruzo?+
Nʼchifukwa chiyani anthu amene amamudziwa sanaone tsiku lake lachiweruzo?
2 Anthu amasuntha zizindikiro za malire.+
Iwo amaba ziweto nʼkuzipititsa pamalo awo odyetsera ziweto.
3 Amathamangitsa bulu wa ana amasiye
Ndipo amalanda ngʼombe yamphongo ya mkazi wamasiye kuti ikhale chikole.+
4 Amachititsa kuti osauka athawe mumsewu.
Anthu ovutika apadziko lapansi amabisala akawaona.+
5 Osaukawo amafunafuna chakudya ngati abulu+ amʼchipululu,
Amafunafuna chakudya cha ana awo mʼchipululu.
6 Amakolola mʼmunda mwa munthu wina
Ndipo amakunkha mʼmunda wa mpesa wa munthu woipa.
7 Osaukawo amakhala usiku wonse ali maliseche,+
Amakhala pamphepo opanda chofunda.
8 Amanyowa ndi mvula mʼmapiri,
Ndipo amakhala pafupi ndi matanthwe chifukwa chakuti alibe pobisala.
9 Oipa amalanda mwana wamasiye kumʼchotsa pabere.+
Ndipo amatenga zovala za osauka kuti zikhale chikole,+
10 Moti amakakamizika kuyenda maliseche,
Komanso amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala.
11 Osaukawo amagwira ntchito mwakhama mʼmigula* ya mʼminda dzuwa likuswa mtengo.*
Amaponda mphesa koma amakhala ndi ludzu.+
12 Anthu amene akufa amakhala akubuula mumzinda.
Anthu amene avulala koopsa amapempha* thandizo,+
Koma Mulungu saona zimenezi ngati zolakwika.*
14 Munthu wopha anthu amadzuka mʼmamawa.
Iye amapha anthu ovutika komanso osauka,+
Ndipo usiku amakhala wakuba.
Ndipo amaphimba nkhope yake.
16 Mumdima anthu oipawo amathyola nyumba za anthu,
Masana amadzitsekera mʼnyumba.
Iwo amadana ndi kuwala.+
17 Kwa iwo mʼmawa nʼchimodzimodzi ndi mdima wandiweyani,
Amadziwa zoopsa zamumdima wandiweyani.
18 Koma iwo amatengedwa mwamsanga ndi madzi.
Malo awo adzakhala otembereredwa.+
Sadzabwerera kuminda yawo ya mpesa.
19 Mofanana ndi madzi amunthaka* amene amauma mʼnyengo yachilimwe komanso kunja kukatentha,
20 Mayi ake adzamuiwala* ndipo mphutsi zidzamudya.
Iye sadzakumbukiridwanso.+
Ndipo kupanda chilungamo kudzathyoledwa ngati mtengo.
21 Iye amachitira zoipa mkazi wosabereka,
Komanso amachitira nkhanza mkazi wamasiye.
22 Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake powononga anthu amphamvu.
Ngakhale atakhala ndi mphamvu, iwo sadziwa ngati angakhalebe ndi moyo kapena ayi.
23 Mulungu amawalola kuti azidzidalira komanso kuti akhale otetezeka.+
24 Oipawo amakhala okwezeka kwa kanthawi, kenako nʼkutha.+
Iwo ali ngati ngala za tirigu zimene zimadulidwa nʼkuikidwa pamodzi.
Amatsitsidwa+ ndipo amafa mofanana ndi anthu ena onse.
25 Choncho ndi ndani amene angapereke umboni wosonyeza kuti ndine wabodza
Kapena kutsutsa mawu angawa?”
25 Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:
2 “Ulamuliro komanso mphamvu zochititsa mantha ndi zake.
Iye amakhazikitsa mtendere kumwamba.*
3 Kodi nʼzotheka kuwerenga asilikali ake?
Ndipo ndi ndani amene saona kuwala kwake?
4 Choncho, kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu,+
Kapena kodi munthu wobadwa kwa mkazi angakhale bwanji wosalakwa?*+
5 Ngakhale mwezi si wowala kwa iye
Ndipo nyenyezi si zoyera mʼmaso mwake,
6 Ndiye kuli bwanji munthu yemwe ndi mphutsi,
Komanso mwana wa munthu yemwe ndi nyongolotsi?”
26 Yobu anayankha kuti:
2 “Komatu ndiye wathandiza munthu wopanda mphamvu!
Wapulumutsa munthu wa manja ofooka.+
3 Waperekadi malangizo othandiza kwa munthu wopanda nzeru.+
Komanso wachititsa kuti anthu ambiri adziwe nzeru zothandiza.
4 Kodi ukuuza ndani,
Ndipo ndi ndani amene wakuuzira zimene ukunenazi?*
5 Akufa alibe mphamvu ndipo amanjenjemera pamaso pa Mulungu.
Iwo ali pansi kwambiri kuposa madzi ndi zonse zimene zimakhala mmenemo.
7 Iye anatambasula thambo lakumpoto* pamwamba pa malo opanda kanthu,+
Ndipo dziko lapansi analiika mʼmalere.
8 Iye anakulunga madzi mʼmitambo yake,+
Mʼnjira yoti mitamboyo isaphulike chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
9 Anaphimba mpando wake wachifumu kuti usamaoneke,
Anauphimba ndi mtambo wake.+
10 Anaika malire pakati pa thambo ndi nyanja,+
Anaika malire pakati pa kuwala ndi mdima.
11 Zipilala zakumwamba zimanjenjemera,
Zimachita mantha ndi kudzudzula kwa Mulungu.
12 Ndi mphamvu zake amavundula nyanja,+
Ndipo ndi kuzindikira kwake amaduladula chilombo cha mʼnyanja.*+
13 Ndi mpweya umene wapuma,* amapangitsa kuti kumwamba kukhale koyera.
Dzanja lake limabaya njoka yothamanga.
14 Komatu zimenezi ndi kambali kakangʼono chabe ka zochita zake,+
Ndipo tangomva kunongʼona kwapansipansi kwa mphamvu zake.
Ndiye ndi ndani amene angamvetse mabingu ake amphamvu?”+
27 Yobu anapitiriza kulankhula* kuti:
2 “Pali Mulungu wamoyo amene wandimana chilungamo,+
Ndiponso pali Wamphamvuyonse amene wachititsa moyo wanga kuti ukhale wowawa,+
3 Ngati ndikupitirizabe kupuma,
Ndiponso mzimu wochokera kwa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,+
4 Milomo yanga sidzalankhula zopanda chilungamo,
Ndipo lilime langa silidzalankhula zachinyengo.
5 Inetu sindingayerekeze nʼkomwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama.
Mpaka ndidzamwalire, sindidzasiya* kukhala wokhulupirika.+
6 Ndipitirizabe kukhala wolungama ndipo sindisiya.+
Mtima wanga sudzanditsutsa* nthawi yonse imene ndidzakhale ndi moyo.*
7 Mdani wanga alangidwe mofanana ndi munthu woipa,
Ndipo wondiukira alangidwe ngati munthu wosalungama.
8 Kodi munthu woipa* akawonongedwa amakhala ndi chiyembekezo chilichonse,+
Mulungu akachotsa moyo wake?
9 Kodi Mulungu adzamva kulira kwake
Mavuto akadzamugwera?+
10 Kapena kodi iye adzasangalala ndi Wamphamvuyonse?
Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?
11 Ndikuphunzitsani zokhudza mphamvu za Mulungu.*
Sindibisa chilichonse chokhudza Wamphamvuyonse.
12 Ngati nonsenu mwaona masomphenya,
Nʼchifukwa chiyani mukulankhula zopanda nzeru?
13 Ili ndi gawo la munthu woipa lochokera kwa Mulungu,+
Cholowa chimene anthu ozunza anzawo amalandira kuchokera kwa Wamphamvuyonse.
14 Ana ake akachuluka, adzaphedwa ndi lupanga,+
Ndipo mbadwa zake sizidzakhala ndi chakudya chokwanira.
15 Mbadwa zake zimene zidzapulumuke zidzaikidwa mʼmanda zitafa ndi mliri,
Ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.
16 Ngakhale ataunjika siliva ngati fumbi,
Nʼkusunga zovala zabwino kwambiri ngati dothi,
17 Ngakhale ataziunjika pamodzi,
Munthu wolungama ndi amene adzazivale,+
Ndipo anthu osalakwa adzagawana siliva wake.
18 Nyumba imene wamanga ndi yosalimba ngati ya kadziwotche,
Ndiponso ngati chisakasa+ chimene mlonda wamanga.
19 Iye adzapita kukagona ali wolemera, koma chuma chake sichidzakhalitsa.
Akadzatsegula maso ake, padzakhala palibe chilichonse.
20 Zoopsa zidzamufikira ngati madzi osefukira.
Chimphepo chamkuntho chidzamuba usiku.+
21 Mphepo yakumʼmawa idzamunyamula nʼkumusowetsa,
Ndipo idzamuchotsa pamalo pake.+
23 Idzamuwombera mʼmanja monyoza
Ndipo idzamuimbira mluzu+ ili pamalo ake.”
28 “Pali malo amene anthu amakumba siliva,
Ndiponso malo amene amakumba golide yemwe amamuyenga.+
2 Chitsulo chimatengedwa munthaka,
3 Munthu amagonjetsa mdima,
Amafufuza mpaka pamapeto mumdima wandiweyani,
Kufunafuna miyala ya mtengo wapatali.
4 Amakumba mgodi kutali ndi kumene anthu amakhala,
Kumalo oiwalika, kutali ndi kumene anthu amayenda.
Anthu ena amatsikira pansi nʼkumagwira ntchito akulendewera.
5 Padziko lapansi pamamera chakudya,
Koma pansi pake pasintha ngati kuti pawonongedwa ndi moto.*
6 Mʼmiyala yake mumapezeka miyala ya safiro,
Ndipo mufumbi lake mumapezeka golide.
7 Mbalame yodya nyama sikudziwa njira yopita kumeneko,
Ndipo diso la mphamba wakuda silinaionepo.
8 Zilombo zamphamvu sizinapondemo,
Mkango wamphamvu sunasakemo nyama.
9 Munthu amaswa mwala wolimba ndi manja ake,
Amagwetsa mapiri kuyambira pansi penipeni.
10 Amapanga ngalande zamadzi+ pathanthwe,
Ndipo maso ake amaona chinthu chilichonse chamtengo wapatali.
11 Kumene mitsinje imayambira, amakumbako madamu,
Ndipo chinthu chobisika amachibweretsa poyera.
13 Palibe munthu amene angadziwe mtengo wake,+
Ndipo nzeru sizingapezeke kulikonse padziko lapansi.
14 Madzi akuya anena kuti,‘Sizili mwa ine.’
Ndipo nyanja yanena kuti, ‘Sizili ndi ine.’+
15 Sizingagulidwe ndi golide woyenga bwino,
Ndipo munthu sangapereke siliva kuti apeze nzeru.+
16 Sangazigule ndi golide wa ku Ofiri,+
Kapena mwala wosowa wa onekisi ndi wa safiro.
17 Nzeru sitingaziyerekezere ndi golide komanso galasi,
Ndipo sitingazisinthanitse ndi mbale ya golide woyenga bwino.+
18 Miyala yamtengo wapatali ya korali ndi kulusitalo sitingaiyerekezere nʼkomwe ndi nzeru.+
Ndipo thumba lodzaza ndi nzeru ndi lamtengo wapatali kuposa thumba lodzaza ndi ngale.
19 Sitingaziyerekezere ndi miyala ya topazi+ ya ku Kusi,
Ngakhale golide woyenga bwino sangagulire nzeru.
20 Koma kodi nzeru zimachokera kuti,
Ndipo kumvetsa zinthu kumachokera kuti?+
21 Zabisika pamaso pa chamoyo chilichonse,+
Ndipo nʼzobisika kwa mbalame zamumlengalenga.
22 Chiwonongeko ndi imfa zanena kuti,
‘Makutu athu angomva lipoti chabe lokhudza nzeruzo.’
23 Mulungu yekha ndi amene amadziwa njira yozipezera,
Iye yekha ndi amene amadziwa kumene zimakhala.+
24 Chifukwa amayangʼana kumapeto kwa dziko lapansi,
Ndipo amaona chilichonse chimene chili pansi pa thambo.+
25 Pamene mphepo ankaipatsa mphamvu,*+
Komanso pamene ankayeza kuchuluka kwa madzi,+
26 Pamene mvula ankaipangira lamulo,+
Komanso pamene ankapanga njira ya mtambo wamvula yamabingu,+
27 Pa nthawi imeneyo iye anaona nzeru pa ntchito imene anagwira nʼkuyamba kuzifotokoza.
Iye anazikhazikitsa nʼkuziyesa.
28 Ndiyeno anauza munthu kuti:
29 Yobu anapitiriza kulankhula* kuti:
2 “Ndikulakalaka ndikanakhala ngati mmene ndinalili mʼmiyezi yapitayi,
Masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,
3 Pamene anachititsa nyale yake kuwala pamutu panga,
Pamene ndinkayenda mumdima iye nʼkumandiunikira ndi kuwala kwake.+
4 Ngati mmene ndinalili ndili mnyamata* komanso ndili ndi mphamvu,
Pa nthawi imene Mulungu anali bwenzi langa lapamtima,+
5 Pamene Wamphamvuyonse anali adakali ndi ine,
Nthawi imene ana* anga onse anali moyo,
6 Pamene ndinkasambitsa mapazi anga mʼmafuta amumkaka,
Ndiponso pamene matanthwe ankanditulutsira mitsinje ya mafuta.+
7 Pa nthawi imene ndinkakonda kupita pageti la mzinda+
Nʼkukakhala pabwalo la mzinda,+
8 Anyamata ankandiona nʼkupatuka,*
Ndipo ngakhale achikulire ankaimirira pondipatsa ulemu.+
9 Akalonga ankakhala chete,
Ndipo ankagwira pakamwa pawo.
10 Anthu olemekezeka sankalankhula,
Lilime lawo linkamatirira mʼkamwa mwawo.
11 Aliyense amene wamva ndikulankhula, ankanena zabwino za ine,
Ndipo amene andiona, ankandichitira umboni.
12 Chifukwa ndinkapulumutsa wosauka amene akupempha thandizo,+
Komanso mwana wamasiye ndi aliyense amene analibe womuthandiza.+
13 Munthu amene watsala pangʼono kufa ankandidalitsa,+
Ndipo ndinkasangalatsa mtima wa mkazi wamasiye.+
14 Ndinkavala chilungamo ngati chovala.
Chilungamo changa chinali ngati mkanjo* komanso nduwira.
15 Ndinali ngati maso kwa munthu amene ali ndi vuto losaona,
Ndipo ndinali ngati mapazi kwa wolumala.
17 Ndinkaphwanya nsagwada za wochita zoipa,+
Ndipo aliyense amene wagwidwa ndi woipayo, ndinkamulanditsa.
18 Ndinkanena kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga,*+
Ndipo masiku anga adzakhala ochuluka ngati mchenga.
19 Mizu yanga idzamwazikana mpaka kukafika mʼmadzi,
Ndipo mame adzakhala usiku wonse panthambi zanga.
20 Anthu adzapitiriza kundilemekeza,
Ndipo uta umene uli mʼmanja mwanga udzapitiriza kuponya mivi.’
21 Anthu ankandimvera ndipo ankandidikirira,
Ankakhala phee kuyembekezera kuti amve malangizo anga.+
22 Ndikamaliza kulankhula, iwo sankalankhulanso.
Ndipo mawu anga ankawasangalatsa.*
23 Iwo ankandidikirira ngati akudikira mvula,
Anali ngati anthu amene akudikirira mwachidwi mvula yomalizira.+
24 Ndikawamwetulira, iwo sankakhulupirira,
Akaona nkhope yanga yosangalala, ankalimbikitsidwa.
25 Ndinkawapatsa malangizo ngati mtsogoleri wawo,
Ndinkakhala ngati mfumu imene ili pakati pa asilikali ake,+
Ndinali ngati wotonthoza anthu amene akulira.”+
30 “Tsopano anthu amene ndi aangʼono kwa ine,
Akundiseka.+
Anthu amene abambo awo sindikanalola
Kuwaika pamodzi ndi agalu olondera nkhosa zanga.
2 Kodi mphamvu za manja awo zinali za ntchito yanji kwa ine?
Nyonga zawo zatha.
3 Iwo atoperatu chifukwa cha njala ndiponso kusowa zinthu.
Amatafuna dera louma
Limene linali lowonongeka kale komanso labwinja.
4 Iwo amathyola chitsamba chamchere mʼtchire,
Ndipo mizu ya mitengo ndi imene inali chakudya chawo.
5 Iwo amathamangitsidwa mʼmudzi.+
Anthu amawakuwiza ngati akuba.
6 Iwo amakhala mʼmalo otsetsereka amʼzigwa,*
Mʼmaenje amʼnthaka ndi mʼmatanthwe.
7 Amalira mokuwa ali pazitsamba
Amaunjikana pansi pa zitsamba zaminga.
8 Monga ana a anthu opusa komanso opanda dzina,
Iwo athamangitsidwa* mʼdziko.
11 Chifukwa Mulungu wandilanda zida* nʼkundipangitsa kuti ndikhale wopanda mphamvu,
Iwo amachita zinthu modzikuza pamaso panga.
12 Iwo aimirira kudzanja langa lamanja ngati gulu la anthu achiwawa kuti andiukire.
Amandichititsa kuti ndithawe,
Koma amanditchingira njira kuti andiwononge.
14 Amabwera ngati akudutsa pampanda umene wagumuka,
Iwo amabwera mwamkokomo mʼmalo owonongeka kale.
15 Zoopsa zandipanikiza.
Ulemu wanga wachoka ngati kuti wauluzika ndi mphepo,
Ndipo chipulumutso changa chachoka ngati mtambo.
18 Chovala changa chakokeka mwamphamvu kwambiri.
Ndipo chikundilepheretsa kupuma mofanana ndi kolala yothina ya chovala changa.
19 Mulungu wandiponya mʼmatope,
Moti ndikungokhala ngati fumbi ndi phulusa.
20 Ndimafuulira kwa inu kuti mundithandize, koma simundiyankha.+
Ndimaimirira, koma inu mumangondiyangʼana.
21 Mwandiukira mwankhanza kwambiri.+
Ndi mphamvu zonse za dzanja lanu, mwandimenya.
22 Mwandinyamula nʼkundiuluza ndi mphepo.
Kenako mwandiponyera uku ndi uku mumphepo yamkuntho.
23 Chifukwa ndikudziwa kuti mudzandipereka ku imfa,
Kunyumba imene aliyense wamoyo adzapitako.
24 Koma palibe amene angamenye munthu amene ali pamavuto*+
Pamene akupempha thandizo pa nthawi ya tsoka.
25 Kodi sindinalirire anthu amene akukumana ndi mavuto?*
Kodi sindinalirire anthu osauka?+
26 Ngakhale kuti ndinkayembekezera zinthu zabwino, zoipa nʼzimene zinabwera.
Ndinkadikirira kuwala, koma kunabwera mdima.
27 Mʼmimba mwanga simunasiye kubwadamuka,
Masiku amasautso anandipeza.
28 Ndikuyendayenda ndili wachisoni+ ndipo dzuwa silikuwala.
Ndaimirira pakati pa mpingo ndipo ndikulira popempha thandizo.
29 Ndakhala mʼbale wake wa mimbulu,
Ndiponso mnzawo wa ana aakazi a nthiwatiwa.+
31 Zeze wanga akungogwiritsidwa ntchito polira,
Ndipo chitoliro changa changokhala choimbira anthu amene akulira.”
31 “Ndachita pangano ndi maso anga.+
Choncho ndingayangʼanitsitse bwanji namwali momusilira?+
2 Kodi ndingalandire gawo lotani kuchokera kwa Mulungu kumwamba?
Kodi cholowa chochokera kwa Wamphamvuyonse mʼmwamba chingakhale chiyani?
3 Kodi si paja wochita zoipa amayembekezera kukumana ndi mavuto,
Ndipo ochita zoipa tsoka limawagwera?+
4 Kodi iye saona njira zanga,+
Ndi kuwerenga masitepe anga onse?
5 Kodi ndinayamba ndanenapo zabodza?
Kodi ndinayamba ndachitirapo aliyense zachinyengo?+
7 Ngati phazi langa lapatuka kusiya njira,+
Kapena ngati mtima wanga watsatira zimene maso anga aona,
Kapenanso ngati manja anga adetsedwa,+
8 Ine ndidzale mbewu wina nʼkudya,+
Ndipo zimene ndinadzala zidzazulidwe.*
9 Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,+
Ndipo ndadikirira+ pakhomo la nyumba ya mnzanga,
10 Mkazi wanga aperere ufa mwamuna wina,
Ndipo amuna ena agone naye.+
11 Chifukwa limenelo lingakhale khalidwe lochititsa manyazi,
Chingakhale cholakwa chimene oweruza akuyenera kundipatsira chilango.+
12 Ungakhale moto umene unganyeketse komanso kuwononga zinthu,*+
Ungapsereze ngakhale mizu ya mbewu* zanga zonse.
13 Ngati ndinalephera kuweruza mwachilungamo kapolo wanga wamwamuna kapena wamkazi
Pamene anali ndi mlandu ndi ine,
14 Ndiye ndingatani Mulungu akamandiweruza?*
Kodi ndingamuyankhe chiyani atandifunsa?+
15 Kodi amene anandipanga mʼmimba si amene anapanganso iwowo?+
Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe tisanabadwe?*+
16 Ngati ndinakana kupatsa osauka zimene ankafuna,+
Kapena kuchititsa kuti mkazi wamasiye amve chisoni,*+
17 Ngati ndinkadya ndekha chakudya changa,
Osagawirako ana amasiye,+
18 (Chifukwa kuyambira ndili mnyamata, ana amasiye akula ndi ine ngati bambo awo,
Ndipo kuyambira ndili mwana* ndakhala ndikuthandiza akazi amasiye.)
19 Ngati ndinkaona munthu akuzunzika ndi mphepo chifukwa chosowa chovala,
Kapena munthu wosauka akusowa chofunda,+
Pamene ankamva kutentha atafunda chofunda cha ubweya wa nkhosa zanga,
21 Ngati ndinaopseza mwana wamasiye ndi chibakera+
Pamene ankafuna kuti ndimuthandize pageti la mzinda,+
22 Mkono wanga ugwe* kuchoka mʼmalo mwake,
Ndipo mkono wanga uthyoke pachigongono.*
23 Chifukwa ine ndinkaopa tsoka lochokera kwa Mulungu,
Ndipo ulemerero wake unkandichititsa mantha.
24 Ngati ndikudalira golide,
Kapena kuuza golide woyenga bwino kuti, ‘Ndimadalira iwe.’+
25 Ngati ndinkasangalala chifukwa chakuti ndinali ndi chuma chochuluka,+
Chifukwa cha zinthu zambiri zimene ndinapeza,+
26 Ngati ndinaona dzuwa likuwala*
Kapena mwezi ukuyenda mwaulemerero,+
27 Ngati mtima wanga unakopeka mwachinsinsi,
Milomo yanga nʼkukisa dzanja langa pozilambira,+
28 Chimenecho chikanakhala cholakwa chimene oweruza akuyenera kundipatsa chilango,
Chifukwa ndikanakhala nditakana Mulungu woona wakumwamba.
29 Kodi ndinayamba ndasangalalapo chifukwa cha kuwonongedwa kwa mdani wanga,+
Kapena kunyadira chifukwa chakuti zoipa zamuchitikira?
30 Ine sindinalole kuti mʼkamwa mwanga muchimwe,
Popempha mochita kulumbira kuti afe.+
31 Kodi amuna amutenti yanga sananene kuti,
‘Ndi ndani amene angabwere ndi munthu amene sanakhute chakudya chake?’*+
32 Palibe mlendo amene ankagona panja usiku.+
Khomo langa linali lotsegula kwa anthu apaulendo.
33 Kodi ndinayamba ndayesapo kubisa zolakwa zanga, ngati anthu ena,+
Pobisa machimo anga mʼthumba la chovala changa?
34 Kodi ndinachitapo mantha ndi zimene gulu la anthu lingachite,
Kapena ndinayamba ndaopa mawu onyoza a mabanja ena,
Nʼkundichititsa kukhala chete komanso kuopa kutuluka panja?
35 Zikanakhala bwino wina akanandimvetsera.+
Ndikanasainira dzina langa pa zimene ndanena.*
Wamphamvuyonse andiyankhe.+
Zikanakhala bwino munthu amene akundiimba mlandu akanalemba milandu yanga papepala.
36 Ndikanalinyamula paphewa langa.
Ndipo ndikanalikulungiza kumutu kwanga ngati chisoti.
37 Ndikanamufotokozera mwatsatanetsatane chilichonse chimene ndinachita.
Ndikanapita kwa iye molimba mtima ngati kalonga.
38 Ngati munda wanga ukanalira modandaula chifukwa cha ine
Ndipo ngati mizere yake ikanalirira pamodzi,
39 Ngati ndadya zipatso zake osalipira,+
Kapena ngati ndachititsa eniake a malowo kuti ataye mtima,+
40 Minga zimere mʼmunda mwanga mʼmalo mwa tirigu
Ndipo mʼmalo mwa balere pamere zitsamba zonunkha.”
Mawu a Yobu athera pamenepa.
32 Choncho amuna atatuwa anasiya kumuyankha Yobu, chifukwa iye ankakhulupirira kuti anali wolungama.*+ 2 Koma Elihu mwana wa Barakeli, mbadwa ya Buza+ wamʼbanja la Ramu anakwiya kwambiri. Iye anakwiyira kwambiri Yobu chifukwa ankadziikira kumbuyo kuti iye ndi wolungama, osati Mulungu.+ 3 Iye anakwiyiranso anzake atatu a Yobu aja chifukwa chakuti sanapeze yankho labwino, mʼmalomwake ankanena kuti Mulungu ndi woipa.+ 4 Elihu anali ndi mawu oti amuyankhe Yobu koma ankadikira kuti anthuwo, amene anali aakulu kwa iyeyo, amalize kulankhula.+ 5 Elihu ataona kuti amuna atatuwo analibe choyankha, anakwiya kwambiri. 6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli mbadwa ya Buza, anayamba kulankhula kuti:
Nʼchifukwa chake mwaulemu ndinakhala chete,+
Ndipo sindinayese nʼkomwe kukuuzani zimene ndikudziwa.
7 Mumtimamu ndinati, ‘Zaka zilankhule.*
Ndipo amene akhala ndi moyo kwa zaka zambiri alankhule zanzeru.’
8 Koma mzimu umene uli mwa anthu,
Mpweya wa Wamphamvuyonse, ndi umene umawathandiza kuti azimvetsa zinthu.+
9 Si zaka zokha zimene zimapangitsa* kuti munthu akhale wanzeru,
Ndipo si achikulire okha amene amadziwa zinthu zoyenera.+
10 Choncho ndikuti, ‘Ndimvetsereni,
Ndipo inenso ndikuuzani zimene ndikudziwa.’
11 Inetu ndimadikira kuti inu mumalize kulankhula.
Ndakhala ndikumvetsera mfundo zanu+
Pamene mumafufuza zoti munene.+
12 Ndakhala ndikukumvetserani mwachidwi,
Koma palibe aliyense wa inu amene wapereka umboni wosonyeza kuti Yobu ndi wolakwa*
Kapena kuyankha zonena zake.
13 Choncho musanene kuti, ‘Tapeza nzeru.
Mulungu ndi amene wamupeza kuti ndi wolakwa, osati munthu.’
14 Iye sanalankhule mawu ondinena,
Choncho ine sindimuyankha potengera mfundo zimene inu mwafotokoza.
15 Iwo achita mantha, mayankho awathera,
Alibenso choti anene.
16 Ine ndadikira, koma sakupitiriza kulankhula.
Iwo angoima, ndipo alibe choyankha.
17 Choncho inenso ndiyankha,
Inenso ndinena zimene ndikudziwa,
18 Chifukwa ndili nʼzambiri zoti ndinene.
Mzimu umene uli mwa ine ukundikakamiza.
19 Ndikungomva ngati ndine* vinyo amene alibe potulukira,
Ngati matumba atsopano a vinyo, amene atsala pangʼono kuphulika.+
20 Ndiloleni ndilankhule kuti ndipeze mpumulo.
Nditsegula pakamwa panga kuti ndiyankhe.
21 Sindikondera wina aliyense,+
Kapena kuyamikira munthu mwachiphamaso,*
22 Chifukwa sinditha kuyamikira munthu mwachiphamaso.
Nditachita zimenezi, amene anandipanga angandichotse mwamsanga.”
33 “Koma tsopano inu a Yobu, imvani mawu anga,
Ndipo mvetserani zonse zimene ndikufuna kunena.
2 Inetu nditsegula pakamwa panga,
Lilime langa likuyenera* kulankhula.
3 Zonena zanga zikusonyeza kuwongoka kwa mtima wanga,+
Ndipo milomo yanga imanena moona mtima zimene ndikudziwa.
5 Ngati mungathe ndiyankheni.
Konzekerani kuti mundifotokozere mfundo zanu.
6 Inetu nʼchimodzimodzi ndi inu pamaso pa Mulungu woona.
Inenso ndinaumbidwa ndi dongo.+
7 Choncho musachite nane mantha,
Ndipo musapanikizike ndi zimene ndikuuzeni.
8 Koma ndakumvani mukunena kuti,
Inde, ndakhala ndikumva mawu anu akuti,
9 ‘Ndine woyera, wopanda tchimo,+
Ndine wosadetsedwa, ndilibe cholakwa.+
10 Koma Mulungu amapeza zifukwa zonditsutsira,
Amandiona ngati mdani wake.+
11 Amaika mapazi anga mʼmatangadza,
Amayangʼanitsitsa njira zanga zonse.’+
12 Koma munalakwitsa ponena zimenezi, choncho ndikuyankhani kuti:
Mulungu ndi wamkulu kwambiri kuposa munthu.+
13 Nʼchifukwa chiyani mukumudandaula?+
Kodi nʼchifukwa chakuti sanakuyankheni mawu anu onse?+
14 Paja Mulungu amalankhula koyamba ndi kachiwiri,
Koma palibe amene amamvetsera.
15 Iye amalankhula mʼmaloto ndi mʼmasomphenya a usiku,+
Anthu akakhala mʼtulo tofa nato,
Akamagona pamabedi awo.
16 Pa nthawi imeneyi mʼpamene amatsegula anthu makutu,+
Ndipo amadinda* malangizo ake mʼmaganizo mwawo,
17 Pofuna kubweza munthu kuti asachite zoipa+
Komanso kumuteteza kuti asakhale wonyada.+
18 Mulungu amateteza moyo wake kuti usapite kudzenje,*+
Amateteza munthu kuti asawonongedwe ndi lupanga.*
19 Munthu amadzudzulidwanso ndi ululu ali pabedi pake,
Ndiponso pamene mafupa ake akumupweteka nthawi zonse,
20 Moti amaipidwa* ndi chakudya,
21 Mnofu wake umatha, osaonekanso,
Ndipo mafupa ake amene samaoneka, amakhala pamtunda.*
22 Moyo wake umayandikira kudzenje.*
Umayandikira amene amabweretsa imfa.
23 Ngati iye ali ndi mthenga,*
Womulankhulira mmodzi pa omulankhulira 1,000,
Kuti auze munthu zimene zili zoyenera,
24 Zikatero Mulungu amamukomera mtima nʼkunena kuti,
25 Mnofu wake usalale* kuposa mmene unalili ali mnyamata.+
Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.’+
26 Adzapemphera kwa Mulungu+ ndipo iye adzamukomera mtima,
Adzaona nkhope yake akufuula mosangalala,
Ndipo Mulungu adzayambanso kuona munthuyo kuti ndi wolungama.
27 Munthu ameneyo adzauza* anthu kuti,
‘Ndachimwa+ komanso kukhotetsa zimene zinali zolungama,
Koma sindinalandire zimene ndimayenera kulandira.*
29 Zoonadi, Mulungu amachitira munthu zinthu zonsezi
Amamuchitira kawiri kapena katatu,
30 Kuti amupulumutse* kudzenje,*
Nʼcholinga choti asangalale ndi moyo.+
31 Tcherani khutu inu a Yobu. Ndimvetsereni!
Khalani chete, ndipo ine ndipitiriza kulankhula.
32 Ngati muli ndi mawu, ndiyankheni.
Lankhulani chifukwa ndikufuna nditsimikizire kuti ndinu wosalakwa.
33 Ngati mulibe mawu alionse, mvetserani mawu anga.
Khalani chete, ndipo ine ndikuphunzitsani kuti mukhale wanzeru.”
34 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:
2 “Mvetserani mawu anga, anthu anzeru inu.
Ndimvetsereni, inu anthu amene mukudziwa zambiri.
3 Chifukwa khutu limasiyanitsa mawu,
Ngati mmene lilime limasiyanitsira* kakomedwe ka chakudya.
4 Tiyeni tifufuze tokha zimene zili zoyenera.
Tisankhe tokha zimene zili zabwino.
6 Kodi ndinganame za mmene chiweruzo changa chimayenera kukhalira?
Chilonda changa sichikupola ngakhale kuti sindinachimwe.’+
7 Kodi pali munthu wina wofanana ndi Yobu,
Amene amamwa mawu onyoza ngati madzi?
8 Iye akuganiza ngati anthu ochita zoipa,
Ndipo akugwirizana ndi anthu oipa.+
9 Chifukwa wanena kuti, ‘Munthu sapindula chilichonse
Akamayesetsa kuchita zosangalatsa Mulungu.’+
10 Choncho ndimvetsereni, inu amuna omvetsa zinthu:*
11 Chifukwa iye amapereka mphoto kwa munthu mogwirizana ndi zimene amachita,+
Ndipo amamusiya kuti akumane ndi mavuto chifukwa cha zochita zake.
13 Ndi ndani anamupatsa udindo woyangʼanira dziko lapansi?
Ndipo ndi ndani anamusankha kuti azilamulira dziko lonse?
14 Iye akakwiyira anthu,
Nʼkutenga mphamvu ya moyo* komanso mpweya wawo,+
15 Anthu onse amafera limodzi,
Ndipo anthuwo amabwerera kufumbi.+
16 Choncho ngati mumamvetsa zinthu, mvetserani izi,
Mvetserani mosamala zimene ndinene.
17 Kodi amene amadana ndi chilungamo angakhale wolamulira,
Kapena kodi munthu wamphamvu amene ndi wolungama, mungamunene kuti ndi woipa?
18 Kodi mungauze mfumu kuti, ‘Ndinu wopanda pake,’
Kapena anthu olemekezeka kuti, ‘Ndinu oipaʼ?+
19 Pali wina amene sakondera akalonga,
Komanso sakondera anthu olemera kuposa osauka,*+
Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+
20 Iwo angafe mwadzidzidzi,+ pakati pa usiku.+
Amaphupha nʼkufa.
Ngakhale anthu amphamvu amawonongedwa, koma osati ndi manja a anthu.+
21 Maso a Mulungu amayangʼanitsitsa njira za munthu,+
Ndipo amaona chilichonse chimene akuchita.
22 Kulibe mdima wandiweyani
Kumene anthu ochita zoipa angathe kubisala.+
23 Chifukwa Mulungu sanaikiretu nthawi yoti munthu aliyense
Akaonekere pamaso pake kuti aweruzidwe.
24 Iye amaphwanya amphamvu ndipo safunikira kufufuza,
Ndipo pamalo awo amaikapo anthu ena.+
26 Amawamenya anthu onse akuona,
Chifukwa choti ndi oipa,+
27 Chifukwa asiya kumutsatira,+
Ndipo salemekeza chilichonse chimene iye akuchita,+
28 Iwo amachititsa kuti osauka amulilire,
Moti amamva kulira kwa anthu ovutika.+
29 Ngati Mulungu atakhala chete, ndi ndani angamudzudzule?
Ngati atabisa nkhope yake, ndi ndani angamuone?
Kaya abisire nkhope yake mtundu wa anthu kapena munthu mmodzi, zotsatira zake nʼchimodzimodzi.
30 Kuti munthu woipa* asalamulire+
Kapena kutchera anthu misampha.
31 Kodi munthu angauze Mulungu kuti,
‘Ndalandira chilango ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse.+
32 Ndiphunzitseni zimene sindikudziwa,
Ngati ndachita cholakwika chilichonse, sindidzachitanso?’
33 Kodi ukufuna kuti akupatse mphoto mogwirizana ndi mmene iweyo ukuonera, pamene ukukana chiweruzo chake?
Iweyo usankhe wekha, osati ine.
Choncho ndiuze zimene ukuzidziwa bwino.
34 Anthu omvetsa zinthu* adzandiuza,
Munthu aliyense wanzeru amene akundimvetsera adzandiuza kuti,
35 ‘Yobu sadziwa zimene akunena,+
Ndipo mawu ake amasonyeza kuti ndi wosazindikira.’
36 Yobu ayesedwe mpaka pamapeto
Chifukwa akuyankha ngati mmene anthu oipa amayankhira.
37 Chifukwa pa tchimo lake akuwonjezerapo kupanduka.+
Amawomba mʼmanja monyogodola ife tikuona
Ndipo amachulukitsa zonena zotsutsana ndi Mulungu woona.”+
35 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:
2 “Kodi mukutsimikiza kuti zimene mukunena nʼzoona moti munganene kuti,
‘Ndine wolungama kuposa Mulunguʼ?+
3 Inu mwanena kuti, ‘Kodi ndikachita zabwino, inu* muli nazo ntchito yanji?
Kodi ndikapanda kuchimwa ndimapindula chiyani?’+
4 Ine ndikuyankhani inuyo
Limodzi ndi anzanu+ amene muli nawowo.
5 Yangʼanani kumwamba muone,
Muonetsetse mitambo+ imene ili kutali ndi inu.
6 Mukachimwa, kodi Mulungu zimamupweteka bwanji?+
Zolakwa zanu zikachuluka, kodi zimamukhudza bwanji Mulungu?+
7 Ngati muli wolungama, kodi mumamʼpatsa chiyani?
Kodi amalandira chiyani kuchokera kwa inu?+
8 Zoipa zimene mumachita zimangopweteka munthu ngati inu nomwe,
Ndipo chilungamo chanu chimangothandiza mwana wa munthu.
9 Ngati anthu akuponderezedwa kwambiri, amalira kuti athandizidwe.
Amalira kuti apulumutsidwe mʼmanja mwa anthu amphamvu amene akuwapondereza.+
10 Koma palibe amene amanena kuti, ‘Kodi Mulungu Wamkulu amene anandipanga+ ali kuti,
Amene amachititsa kuti tiziimba nyimbo usiku?’+
11 Iye amatiphunzitsa+ zinthu zambiri kuposa nyama zakutchire,+
Ndipo amatipatsa nzeru kuposa mbalame zamumlengalenga.
14 Ndiye kodi iye angamvetsere mukamadandaula kuti simukumuona?+
Iye ndi amene angaweruze mlandu wanu, choncho muzimuyembekezera.+
15 Pajatu iye sanakukwiyireni nʼkukupatsani chilango,
Komanso sanaone kudzitukumula kwanu.+
16 Choncho Yobu watsegula pakamwa pake mopanda phindu.
Ngakhale kuti sakudziwa zoona, iye akulankhula zambirimbiri.”+
36 Elihu anapitiriza kunena kuti:
2 “Ndilezereni mtima kwa kanthawi kochepa kuti ndifotokoze,
Chifukwa ndidakali ndi mawu oti ndinene mʼmalo mwa Mulungu.
3 Ndifotokoza mwatsatanetsatane zimene ndikudziwa,
Ndipo ndinena kuti amene anandipanga, ndi wachilungamo.+
4 Ndikunena zoona, mawu anga si onama.
Amene amadziwa chilichonse+ akukuonani.
5 Inde, Mulungu ndi wamphamvu+ ndipo sakana munthu aliyense.
Iye ali ndi mphamvu zazikulu zomvetsa zinthu.*
7 Iye sasiya kuyangʼanitsitsa wolungama.+
Amawaika kukhala mafumu,+ ndipo amalemekezeka mpaka kalekale.
8 Koma akamangidwa mʼmatangadza,
Nʼkugwidwa ndi zingwe zamavuto,
9 Iye amawaululira zimene achita,
Zimene alakwitsa chifukwa cha kunyada kwawo.
10 Iye amatsegula makutu awo kuti awapatse malangizo
Ndi kuwauza kuti asiye kuchita zoipa.+
11 Akamamumvera komanso kumutumikira,
Zinthu zidzawayendera bwino pa nthawi yonse ya moyo wawo,
Ndipo moyo wawo udzakhala wosangalatsa.+
13 Anthu oipa mtima* adzasunga chakukhosi.
Iwo sapempha thandizo ngakhale Mulungu atawamanga.
15 Koma Mulungu amapulumutsa anthu ovutika pa mavuto awo,
Amatsegula makutu awo akamaponderezedwa.
16 Iye amakukokani mukatsala pangʼono kukumana ndi mavuto+
Nʼkukupititsani pamalo otakasuka, opanda mavuto.+
Patebulo panu pali chakudya chambiri chabwino chimene chimakusangalatsani.+
17 Kenako mudzakhutira ndi chiweruzo chimene chidzaperekedwe kwa oipa.+
Pa nthawi imene chiweruzo chidzaperekedwe komanso chilungamo chidzatsatiridwe.
18 Samalani kuti mkwiyo usakuchititseni zinthu mwanjiru,*+
Ndipo musalole kuti akupatseni ziphuphu zambiri nʼkukusocheretsani.
19 Kodi kulira kwanu kopempha thandizo
Kapena kuyesetsa kwanu mwamphamvu kungakuthandizeni kuti musakumane ndi mavuto?+
20 Musamalakelake kuti usiku ufike,
Pamene anthu amasowa pamalo awo.
21 Samalani kuti musayambe kuchita zinthu zoipa,
Musasankhe zimenezi mʼmalo mwa mavuto.+
22 Pajatu Mulungu ali ndi mphamvu zapamwamba.
Kodi pali mphunzitsi winanso wofanana naye?
23 Ndi ndani anauzapo Mulungu kuti chitani izi,+
Kapena ndi ndani amene anamuuza kuti, ‘Zimene mwachitazi ndi zolakwikaʼ?+
25 Anthu onse aziona,
Munthu amaziyangʼana ali patali.
26 Inde Mulungu ndi wamkulu kuposa mmene tikudziwira.+
27 Iye amakoka madontho a madzi.+
Madonthowo amasintha nʼkukhala nkhungu imene imapanga mvula,
28 Kenako mitambo imagwetsa mvula,+
Imagwetsera aliyense madzi.
29 Kodi alipo amene angamvetse mmene mitambo anaitambasulira,
31 Pogwiritsa ntchito zimenezi, iye amapereka chakudya kwa anthu onse.
Amawapatsa chakudya chochuluka.+
32 Iye amafumbata mphezi mʼmanja mwake,
Ndipo amailamula kuti ikagwere pamene akufuna.+
33 Mabingu ake amanena za iye,
Ngakhale ziweto zimadziwa amene akubwera.”
37 “Chifukwa cha zimenezi, mtima wanga ukugunda kwambiri,
Ukungokhala ngati uchoka mʼmalo mwake.
2 Mvetserani mwatcheru mawu amphamvu a Mulungu,
Komanso mabingu ochokera mʼkamwa mwake.
3 Amene amamveka pansi ponse pa thambo,
Ndipo amatumiza mphezi yake+ kumalekezero a dziko lapansi.
4 Pambuyo pake pamamveka phokoso.
Iye amabangula ndi mawu amphamvu,+
Ndipo mphezi zimakhala zikuwala iye akamalankhula.
5 Mulungu amabangula ndi mawu ake+ mochititsa chidwi kwambiri.
Amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.+
6 Chifukwa amauza matalala kuti, ‘Gwerani padziko lapansi,’+
Ndipo mvula amaiuza kuti, ‘Igwa mwamphamvu kwambiri.’+
7 Mulungu amaimitsa chilichonse chimene anthu akuchita,*
Kuti munthu aliyense adziwe ntchito Yake.
8 Nyama zakutchire zimapita mʼnyumba zawo,
Ndipo zimakhalabe mʼmalo amene zimakhala.
10 Pogwiritsa ntchito mpweya wake Mulungu amapangitsa kuti madzi aundane,+
Komanso kuti madzi aundane chifukwa cha kuzizira.+
11 Iye amachititsa kuti mitambo ilemedwe ndi chinyontho.
Amamwaza mphezi+ zake mʼmitambo.
12 Mitamboyo imayenda mozungulira ndipo iye amailamula kuti ipite kumene akufuna.
Imachita chilichonse chimene iye walamula+ panthaka yapadziko lapansi.*
13 Amagwiritsa ntchito mitamboyo kuti apereke chilango,*+ kuti anyowetse dziko,
Komanso kuti asonyeze chikondi chokhulupirika.+
14 Mvetserani izi inu a Yobu,
Imani ndi kuganizira mozama ntchito zodabwitsa za Mulungu.+
15 Kodi mukudziwa zimene Mulungu amachita kuti alamulire mitambo
Komanso zimene amachita kuti mphezi ziziwala mʼmitambo yake?
16 Kodi mukudziwa chimene chimachititsa kuti mitambo izikhala mʼmalere?+
Zimenezi ndi ntchito zodabwitsa za Mulungu amene amadziwa chilichonse.+
17 Nʼchifukwa chiyani zovala zanu zimatentha,
Pamene mphepo yakumʼmwera yachititsa dziko lapansi kuti likakhale bata?+
18 Kodi inuyo limodzi ndi iyeyo mungatambasule kuthambo,+
Nʼkukumenyamenya kuti kukhale kolimba ngati chitsulo chonyezimira?*
19 Tiuzeni zoti timuuze.
Sitingathe kuyankha chifukwa tili mumdima.
20 Kodi auzidwe kuti ndikufuna kulankhula?
Kapena kodi munthu wina wanena zinazake zimene akufunika kuti auzidwe?+
21 Iwo sangathe nʼkomwe kuona kuwala,*
Ngakhale kuti kuthambo nʼkowala,
Mpaka mphepo itadutsa nʼkuchotsa mitambo.
22 Ulemerero wonyezimira ngati golide umachokera kumpoto.
Ulemerero wa Mulungu+ ndi wochititsa mantha.
23 Wamphamvuyonse sitingathe kumumvetsa.+
Iye ali ndi mphamvu zazikulu,+
Ndipo sachita zinthu zosemphana ndi chilungamo+ chake komanso kulungama kwake kodabwitsa.+
24 Choncho anthu azimuopa.+
Chifukwa sakondera aliyense amene amadziona kuti ndi wanzeru.”*+
38 Kenako Yehova anayankha Yobu kudzera mumphepo yamkuntho kuti:+
2 “Kodi uyu ndi ndani amene akuphimba malangizo angayu
Nʼkumalankhula mopanda nzeru?+
3 Konzeka ngati mwamuna wamphamvu.
Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.
4 Kodi unali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi?+
Ndiuze ngati ukudziwa mmene zinakhalira.
5 Ndi ndani amene anaika miyezo yake, ngati ukudziwa,
Kapena ndi ndani analiyeza ndi chingwe choyezera?
6 Kodi zipilala zake zinazikidwa pachiyani?
Kapena ndi ndani amene anaika mwala wake wapakona,+
7 Pamene nyenyezi zamʼmawa+ zinafuula pamodzi mosangalala,
Ndiponso pamene ana onse a Mulungu*+ anayamba kufuula mosangalala?
8 Ndi ndani anatseka nyanja ndi zitseko,+
Pamene inaphulika kuchokera mʼmimba,
9 Pamene ndinaiveka mitambo
Nʼkuikulunga mumdima wandiweyani,
10 Pamene ndinaiikira malire,
Nʼkuiikiranso mpiringidzo ndi zitseko zake,+
11 Ndiye ndinati, ‘Ukhoza kufika apa, koma usapitirirepo,
Ndipo mafunde ako aatali azilekezera pamenepaʼ?+
12 Kodi unayamba* walamulapo mʼmawa
Kapena kuchititsa kuti mʼbandakucha udziwe malo ake,+
13 Kuti kuwala kwake kufike mpaka kumalekezero a dziko lapansi,
Nʼkuthamangitsa anthu oipa kuti achokemo?+
14 Dzikolo limasintha ngati dongo limene ladindidwa ndi chodindira,
Ndipo limaoneka ngati chovala chokongola cha mitundu yosiyanasiyana.
15 Koma kuwala kwa oipa kwachotsedwa,
Ndipo dzanja lawo limene analikweza mʼmwamba lathyoledwa.
16 Kodi unayamba wafika kumene kuli akasupe a nyanja
Kapena kodi unayamba wafufuzapo zimene zili pansi pa nyanja zakuya?+
17 Kodi anayamba akuululira kumene kuli mageti a imfa,+
18 Kodi ukudziwa bwino kukula kwa dziko lapansi?+
Ndiuze ngati ukudziwa zonsezi.
19 Kodi kuwala kumakhala kuti kwenikweni,+
Nanga mdima umakhala kuti?
20 Kodi ungazipititse kumalo awo,
Komanso kodi ukudziwa njira zopita kunyumba kwawo?
21 Kodi ukudziwa zimenezi chifukwa choti pa nthawiyo unali utabadwa,
Komanso chifukwa chakuti uli ndi zaka zambiri?*
22 Kodi unalowapo mʼnyumba zosungira madzi oundana,+
Kapena unaonapo nyumba zosungira matalala,+
23 Zimene ndazisunga kuti ndidzazigwiritse ntchito pa nthawi ya mavuto aakulu,
Pa tsiku lomenyana komanso lankhondo?+
24 Kodi kuwala kumamwazikana* kuchokera kuti,
Ndipo kodi mphepo yakumʼmawa imawomba padziko lapansi kuchokera kuti?+
25 Ndi ndani anatsegula ngalande za madzi a mvula kuthambo,
Nʼkupanga njira ya mtambo wa mvula yamabingu,+
26 Kuti achititse mvula kugwa kumalo amene sikukhala munthu,
Kuchipululu kumene kulibe anthu,+
27 Kuti inyowetse chipululu chouma chomwe ndi chowonongeka,
Nʼkuchititsa kuti udzu umere?+
29 Kodi madzi oundana amachokera mʼmimba mwa ndani,
Ndipo ndi ndani amene anabereka nkhungu yamumlengalenga?+
30 Kodi ndi ndani amene amachititsa chivundikiro cha madzi kuti chikhale cholimba ngati mwala,
Komanso kuti madzi amene ali pamwamba pa madzi akuya aundane chifukwa chozizira?+
31 Kodi ungamange zingwe za gulu la nyenyezi la Kima
Kapena kumasula zingwe za gulu la nyenyezi la Kesili?+
32 Kodi ungatulutse gulu la nyenyezi* pa nyengo yake
Kapena kutsogolera gulu la nyenyezi la Asi* pamodzi ndi ana ake?
33 Kodi ukudziwa malamulo amene zinthu zakuthambo zimatsatira,+
Kapena kodi ungaike ulamuliro wake padziko lapansi?
34 Kodi ungafuulire mitambo
Kuti igwetse mvula yamphamvu nʼkukunyowetsa?+
35 Kodi ungatumize mphezi kuti zikagwire ntchito yake?
Kodi zingabwere kwa iwe nʼkudzakuuza kuti, ‘Ife tabwerakoʼ?
36 Ndi ndani anaika nzeru mʼmitambo,*+
Kapena ndi ndani anachititsa kuti zinthu zakuthambo zikhale zozindikira?*+
37 Ndi ndani amene ali wanzeru kwambiri moti angawerenge mitambo,
Kapena ndi ndani amene angapendeketse zosungira madzi zakumwamba?+
38 Ndi ndani amene amachititsa kuti fumbi lisanduke matope,
Komanso kuti zibuma zadothi zimatane?
39 Kodi mkango ungausakire nyama,
Kapena kuthetsa njala ya mikango yamphamvu?+
40 Kodi ungaipatse chakudya pamene yamyata mʼmalo amene imabisala,
Kapena pamene yabisalira nyama mʼnyumba zawo?
41 Ndi ndani amakonzera khwangwala chakudya,+
Ana ake akamalirira Mulungu kuti awathandize,
Komanso akamadzandira chifukwa chosowa chakudya?”
39 “Kodi ukudziwa nthawi imene mbuzi zamʼmapiri zimabereka?+
Kodi unayamba waona mphoyo zikubereka?+
2 Kodi umawerenga miyezi imene imadutsa zili ndi bere?
Kodi ukudziwa nthawi imene zimabereka?
3 Zimagwada zikamaswa ana awo,
Ndipo ululu wawo wapobereka umatha.
4 Ana awo amakhala amphamvu ndipo amakulira mʼtchire.
Amachoka osabwereranso kwa makolo awo.
5 Ndi ndani anapatsa bulu wamʼtchire ufulu womangodziyendera,+
Ndipo ndi ndani amene anamasula zingwe za bulu wamʼtchire?
6 Ndinamupatsa chipululu kuti ikhale nyumba yake,
Ndiponso dera la nthaka yamchere kuti akhale malo ake okhala.
7 Amapewa phokoso lamumzinda,
Ndipo samva mawu a munthu amene amalamula nyama kuti zigwire ntchito.
8 Amayendayenda mʼmapiri pofunafuna msipu,
Ndipo amafunafuna chomera chilichonse chobiriwira.
9 Kodi ngʼombe yamphongo yamʼtchire imafunitsitsa kukutumikira?+
Kodi ingagone usiku wonse mʼkhola lako?*
10 Kodi ungamange ngʼombe yamʼtchire ndi zingwe kuti ikulimire mizere,
Kapena kodi ingalole kuti upite nayo kuchigwa kukalima?
11 Kodi ungaikhulupirire chifukwa ili ndi mphamvu zochuluka,
Nʼkuisiya kuti ikugwirire ntchito yako yotopetsa?
12 Kodi ungaidalire kuti ikubweretsere zokolola zako?
Ndipo kodi ingatenge zokololazo nʼkupita nazo pamalo opunthira?
13 Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake mosangalala,
Koma kodi mapiko ndi nthenga zake nʼzofanana ndi za dokowe?+
14 Imasiya mazira ake munthaka,
Ndipo imawatenthetsa mumchenga.
15 Imaiwala kuti phazi linalake likhoza kuwaphwanya,
Kapenanso kuti nyama yakutchire ikhoza kuwaponda.
16 Imachitira nkhanza ana ake ngati kuti si ake,+
Ndipo siopa kuti ntchito imene yagwira powasamalira ingakhale yopanda phindu.
17 Chifukwa Mulungu sanaipatse* nzeru
Ndipo sanaipange kuti izichita zinthu mozindikira.
18 Koma ikaimirira nʼkutambasula mapiko ake kuti ithawe,
Imaseka hatchi ndi wokwerapo wake.
19 Kodi ndi iwe amene umapereka mphamvu kwa hatchi?+
Kodi ndi iwe amene umaveka khosi lake manyenje awirawira?
20 Kodi ungaichititse kuti idumphe ngati dzombe?
Phokoso lamphamvu limene imatulutsa mʼmphuno mwake ndi lochititsa mantha.+
21 Imachita mgugu mʼchigwa, ndipo imasangalala ndi mphamvu zake.+
22 Imanyoza mantha ndipo siopa chilichonse.+
Sibwerera mʼmbuyo chifukwa choopa lupanga.
23 Kachikwama koika mivi kamachita phokoso kakamagunda mʼnthiti mwake,
Mkondo ndi nthungo yake zimanyezimira.
24 Imathamangira kutsogolo* ikunjenjemera chifukwa chosangalala.
Ndipo singaime chifukwa choti yamva phokoso la lipenga.
25 Lipenga likangolira imati, ‘Eyaa!’
Imanunkhiza nkhondo ili kutali,
Ndipo imamva kufuula kwa atsogoleri a asilikali komanso phokoso la nkhondo.+
26 Kodi nzeru zako ndi zimene zimachititsa kuti kabawi auluke,
Komanso atambasulire mapiko ake kumʼmwera?
27 Kapena kodi chiwombankhanga chimauluka mʼmwamba chifukwa choti iweyo wachilamula,+
Nʼkukamanga chisa chake pamwamba kwambiri?+
28 Chimagona kuphedi usiku wonse,
Ndipo chimakhala mʼmalo ake otetezeka kuphanga lapathanthwe.*
29 Chili pamalo omwewo, chimafunafuna chakudya,+
Maso ake amaona kutali kwambiri.
30 Ana ake amamwa magazi.
Ndipo kumene kuli zakufa, ichonso chimakhala komweko.”+
40 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Yobu kuti:
2 “Kodi opezera ena chifukwa ayenera kutsutsana ndi Wamphamvuyonse?+
Amene akufuna kudzudzula Mulungu ayankhe.”+
3 Ndiyeno Yobu anayankha Yehova kuti:
4 “Ine ndine wopanda pake.+
Kodi ndingakuyankheni chiyani?
Ndaika dzanja langa pakamwa.+
5 Ndalankhula kambirimbiri.
Koma pano sindiyankha kapena kunena chilichonse.”
6 Ndiyeno Yehova anayankha Yobu kudzera mumphepo yamkuntho kuti:+
7 “Konzeka ngati mwamuna wamphamvu.
Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+
8 Kodi unganene kuti ndine wopanda chilungamo?
Kodi ungandiweruze kuti ndine wolakwa kuti iweyo ukhale wolondola?+
9 Kodi uli ndi dzanja lamphamvu ngati la Mulungu woona?+
Kapena kodi mawu ako angagunde ngati mabingu mofanana ndi mawu a Mulungu?+
10 Udziveke ulemerero ndiponso mphamvu,
Ndipo uvale ulemu ndi ulemerero.
11 Utulutse mkwiyo wonse umene uli nawo,
Yangʼana aliyense amene ndi wodzikweza ndipo umutsitse.
12 Yangʼana aliyense wodzikweza ndipo umutsitse,
Ndipo oipa uwaponderezere pamalo amene ali.
13 Uwabise onse mufumbi,
Uwamange* nʼkuwaika mʼmalo amdima,
14 Ukatero ngakhale ine ndidzavomereza*
Kuti dzanja lako lamanja lingakupulumutse.
15 Ine ndinapanga mvuu* ndipo ndinapanganso iweyo.
Iyo imadya udzu ngati ngʼombe yamphongo.
16 Mphamvu zake zili mʼchiuno mwake,
Ndipo minofu yapamimba pake ndi yamphamvu kwambiri.
17 Imalimbitsa mchira wake ngati mtengo wa mkungudza,
Mitsempha yamʼntchafu zake ndi yolukanalukana.
18 Mafupa ake ali ngati mapaipi akopa,*
Miyendo yake ili ngati ndodo zachitsulo.
19 Iyo ndi yoyamba komanso yaikulu kwambiri pa nyama zamtundu umenewu zimene Mulungu analenga.
Amene anaipanga ndi yekhayo amene angaiyandikire ndi lupanga.
20 Mapiri amaipatsa chakudya,
Ndipo nyama zonse zakutchire zimasewera mmenemo.
21 Imagona pansi pa mitengo yaminga,
Pamthunzi wa mabango amʼmadambo.
22 Mitengo yaminga imaipatsa mthunzi,
Ndipo imazunguliridwa ndi mitengo ya msondodzi yamʼchigwa.*
23 Mtsinje ukadzaza, iyo sichita mantha.
Imalimba mtima ngakhale madzi a mu Yorodano+ atasefukira nʼkumaimenya kumaso.
24 Kodi alipo amene angaigwire iyo ikuona
Kapena kubowola mphuno yake ndi ngowe?”*
3 Kodi iyo ingakuchonderere kambirimbiri,
Kapena kodi ingalankhule nawe mofatsa?
4 Kodi ingachite nawe pangano,
Kuti ikhale kapolo wako moyo wake wonse?
5 Kodi ungasewere nayo ngati mbalame,
Kapena kodi ungaimange pachingwe kuti izisangalatsa ana ako aakazi?
6 Kodi ochita malonda angaigulitse posinthanitsa ndi chinthu china?
Kodi angaiduledule nʼkuigawa kwa amalonda?
8 Igwire ndi dzanja lako,
Sudzaiwala ikadzakuukira ndipo sudzabwerezanso.
9 Kuyembekezera kuti ungaigonjetse nʼkungotaya nthawi.
Kungoiona kokha umachita mantha.*
10 Palibe angalimbe mtima kuti aipute.
Ndiye ndi ndani amene angaimitsane ndi ine?+
11 Ndi ndani anandipatsapo chinthu chilichonse kuti ndimubwezere?+
Chilichonse chimene chili pansi pa thambo ndi changa.+
12 Sindikhala chete osanena za miyendo yake,
Zokhudza mphamvu zake ndi thupi lake loumbidwa bwino.
13 Ndi ndani anachotsa chikopa chake cholimba?
Ndi ndani angalowe pakati pa nsagwada zake itayasamula?
14 Ndi ndani angatsegule zitseko zapakamwa pake?*
Mano ake onse ndi ochititsa mantha.
15 Pamsana pake pali mizere ya mamba
Amene ndi othithikana kwambiri.
16 Ndi othithikana kwambiri,
Moti ngakhale mpweya sungadutse pakati pawo.
17 Ndi omatirirana,
Anaphatikana ndipo sizingatheke kuwalekanitsa.
18 Ikayetsemula pamaoneka kuwala,
Ndipo maso ake ali ngati kuwala kwa mʼbandakucha.
19 Mʼkamwa mwake mumatuluka kungʼanima kwa mphezi,
Komanso mumathetheka moto.
20 Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi,
Ngati ngʼanjo imene yayatsidwa ndi udzu.
21 Mpweya wake umayatsa makala,
Ndipo mʼkamwa mwake mumatuluka lawi la moto.
22 Mʼkhosi mwake muli mphamvu zochuluka,
Ndipo onse amene akumana nayo amachita mantha kwambiri.
23 Minofu yake ndi yokwinyikakwinyika komanso yothithikana.
Ndi yolimba ngati kuti anaiumbira pomwepo ndipo sisuntha.
24 Mtima wake ndi wolimba ngati mwala.
Inde ndi wolimba ngati mwala wa mphero.
25 Ikadzuka, ngakhale anthu amphamvu amachita mantha.
Ikamagwedeza mchira wake imachititsa mantha.
26 Palibe amene angaigonjetse ndi lupanga,
Ngakhalenso mkondo, mpaliro, kapena muvi.+
27 Chitsulo imangochiona ngati udzu,
Ndipo kopa imangomuona* ngati mtengo wowola.
28 Muvi suipangitsa kuti ithawe.
Miyala yoponya ndi gulaye* imasanduka mapesi kwa iyo.
29 Chibonga imangochiona ngati phesi,
Ndipo imaseka ikamva phokoso la nthungo.
30 Kumimba kwake kuli ngati timapale tosongoka.
Ikagona mʼmatope imakhala ngati chopunthira mbewu.+
31 Imachititsa madzi akuya kuwira ngati ali mumphika.
Imatakasa nyanja ngati mphika wa mafuta onunkhira.
32 Ikamasambira imasiya madzi a thovu mʼmbuyo mwake.
Moti munthu angaganize kuti madzi achita imvi.
33 Padziko lapansi palibe chofanana nayo.
Mulungu anaipanga kuti isamachite mantha.
34 Imayangʼana mopanda mantha nyama iliyonse yodzikweza.
Iyo ndi mfumu ya zilombo zonse zakutchire, zomwe ndi zamphamvu.”
42 Kenako Yobu anayankha Yehova kuti:
2 “Tsopano ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse,
Ndiponso kuti palibe chilichonse chimene mukufuna kuchita chimene simungakwanitse.+
3 Inu munati, ‘Kodi uyu ndi ndani amene akuphimba malangizo anga nʼkumalankhula mopanda nzeruyu?’+
Choncho ndinalankhula, koma mosazindikira
Zokhudza zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine, zimene sindikuzidziwa.+
4 Inu munati, ‘Tamvera, ndikufuna ndilankhule.
Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.’+
5 Makutu anga anamva za inu,
Koma tsopano ndikukuonani ndi maso angawa.
7 Yehova atanena mawu amenewa kwa Yobu, Yehova anauza Elifazi wa ku Temani kuti:
“Mkwiyo wanga wayakira iweyo ndi anzako awiriwo,+ chifukwa simunanene zoona za ine,+ ngati mmene wachitira mtumiki wanga Yobu. 8 Tsopano utenge ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7. Upite nazo kwa mtumiki wanga Yobu, ndipo inuyo mukapereke nsembe yopsereza chifukwa cha tchimo lanu. Ndiyeno Yobu mtumiki wanga akakupemphererani.+ Ndithudi ineyo ndidzayankha pempho lake* kuti ndisakuchitireni zinthu mogwirizana ndi zopusa zimene mwachita, chifukwa simunanene zoona zokhudza ine ngati mmene wachitira mtumiki wanga Yobu.”
9 Choncho Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Shuwa ndi Zofari wa ku Naama anapita nʼkukachita zimene Yehova anawauza. Ndipo Yehova anamva pemphero la Yobu.
10 Yobu atapempherera anzake aja,+ Yehova anathetsa mavuto a Yobu+ nʼkubwezeretsa chuma chimene anali nacho.* Yehova anamupatsa zonse zimene anali nazo, kuwirikiza kawiri.+ 11 Azichimwene ndi azichemwali ake onse komanso anzake onse akale+ anapita kwa iye ndipo anadya naye limodzi chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamulimbikitsa komanso kumupepesa chifukwa cha masoka onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwo anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.
12 Yehova anadalitsa kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake+ moti iye anakhala ndi nkhosa 14,000, ngamila 6,000, ngʼombe 2,000* ndi abulu aakazi 1,000.+ 13 Anakhala ndi ana enanso aamuna 7 ndi ana aakazi atatu.+ 14 Mwana wake wamkazi woyamba anamʼpatsa dzina lakuti Yemima, wachiwiri Keziya ndipo wachitatu Kereni-hapuki. 15 Mʼdziko lonselo munalibe akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, ndipo bambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi azichimwene awo.
16 Pambuyo pa zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140 ndipo anaona ana ake ndi zidzukulu zake mpaka mʼbadwo wa 4. 17 Pomalizira pake Yobu anamwalira atakhala ndi moyo wautali komanso wosangalatsa.*
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Munthu Wodedwa.”
Kapena kuti, “munthu wopanda cholakwa komanso wamtima wowongoka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “abulu aakazi 500.”
Kapena kuti, “kunyumba kwa aliyense tsiku lake likafika.”
Mawu okuluwika a Chiheberi onena za angelo omwe ndi ana a Mulungu.
Kapena kuti, “munthu wopanda cholakwa komanso wamtima woongoka.”
Mabaibulo ena amati, “Mphezi inatsika.”
Kapena kuti, “kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.”
Mawu okuluwika a Chiheberi onena za angelo omwe ndi ana a Mulungu.
Kapena kuti, “munthu wopanda cholakwa komanso wamtima wowongoka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimumeze.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuwononga fupa ndi mnofu wake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yobu sanachimwe ndi milomo yake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kutemberera tsiku lake.”
Kapena kuti, “Mdima ndi mthunzi wa imfa zilitenge.”
Kapena kuti, “amene amakonza.”
Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”
Kapena kuti, “amithenga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “woyera.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakuwombola.”
Kapena kuti, “idzachita pangano (mgwirizano) ndi iwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tenti yako ili pa mtendere.”
Kapena kuti, “zopanda pake; zopanda nzeru.”
Kapena kuti, “kuti nditalikitse moyo wanga.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “Gulu la Asabeya apaulendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mundiwombole.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zabwino.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuika mtima wanu pa iye?”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye anawapereka mʼmanja mwa kupanduka kwawo.”
Kapena kuti, “Iye akanadzuka kuti akumvere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzatulutsa mawu kuchokera mʼmitima yawo?”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mmenemu ndi mmene zilili njira za.”
Kapena kuti, “ampatuko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba ya kangaude.”
Kapena kuti, “akamezedwa.”
Kapena kuti, “Umu ndi mmene njira yake idzathere.”
Kapena kuti, “anthu opanda cholakwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kugwira dzanja la.”
Kapena kuti, “akufuna kutengera Mulungu kukhoti.”
Kapena kuti, “Iye amachotsa.”
Nʼkutheka kuti chimenechi ndi chilombo choopsa cha mʼnyanja.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndi ndani angandisumire?”
Kapena kuti, “Ngakhale nditakhala wosalakwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzapezabe kuti ndine wokhotakhota.”
Kapena kuti, “Ngakhale nditakhala wosalakwa.”
Kapena kuti, “ndikuunyoza; ndikuukana.”
Kapena kuti, “okhulupirika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nkhope za oweruza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “woipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmadzi achipale chofewa.”
Kapena kuti, “Palibe mʼkhalapakati pa mlandu wathu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amene angaike dzanja lake patonsefe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngati iye akanachotsa ndodo yake pa ine.”
Kapena kuti, “Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.”
Tchizi ndi chakudya chopangidwa kuchokera ku mkaka.
Kapena kuti, “mumateteza moyo wanga; mumateteza mpweya wanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo zinthu zimenezi mwazibisa mumtima mwanu.”
Kapena kuti, “ndisangalaleko pangʼono.”
Kapena kuti, “Kudziko lamdima komanso mthunzi wa imfa.”
Kapena kuti, “Kapena kodi munthu wodzitama angakhale wosalakwa?”
Kapena kuti, “ungadziwe malire a kukula kwa.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kutha kwa moyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu inu ndinu anthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inenso ndili ndi mtima.”
Kapena kuti, “anthu okhawo amene mapazi awo aterereka.”
Mabaibulo ena amati, “lankhula.”
Kapena kuti, “mpweya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼkamwa mumasiyanitsira.”
Kapena kuti, “ayende atavulidwa chilichonse.”
Kapena kuti, “kwa akulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo amakhwepetsa lamba wa anthu amphamvu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amachotsa mtima wa atsogoleri.”
Kapena kuti, “Kodi mumukondera iyeyo?”
Kapena kuti, “osaiwalika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nʼchifukwa chiyani ndikunyamula mnofu wanga ndi mano.”
Kapena kuti, “Ndingaikire kumbuyo njira zanga.”
Kapena kuti, “wampatuko.”
Mabaibulo ena amati, “Ngati alipo, ine ndikhala chete nʼkufa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Zinthu ziwiri zokha musandichitire.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “iye,” mwina kutanthauza Yobu.
Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mukundizenga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi munthu woyera angabadwe kwa munthu wodetsedwa?”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “angayankhe ndi nzeru zokhala ngati mphepo.”
Kapena kuti, “Zolakwa zako zimaphunzitsa pakamwa pako.”
Kunenepa kumeneku kukuimira kuti munthuyu zinthu zikumuyendera bwino, amachita zinthu mosadziletsa komanso ndi wodzikuza.
Chimene ndi chiyembekezo chilichonse choti adzachira.
Kapena kuti, “ampatuko.”
Kapena kuti, “Kodi simusiya kulongololaku?”
Kapena kuti, “Moyo wanu ukanakhala ngati mmene moyo wanga ulili.”
Kapena kuti, “onse osonkhana nane.”
Kapena kuti, “mphamvu yanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga yanga.”
Kapena kuti, “pali mthunzi wa imfa.”
Kapena kuti, “likuyenera kukhala pa.”
Kapena kuti, “ampatuko.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “manda.”
Apa akunena chiyembekezo.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “anthu odetsedwa.”
Kapena kuti, “motsimphina.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwana woyamba kubadwa wa imfa wagwira.”
Kapena kuti, “adzamupititsa ku imfa yowawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Chinthu chomwe si chake chidzakhala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzakhala ndi dzina.”
Kapena kuti, “pamalo amene akukhala monga mlendo.”
Kapena kuti, “mwakhala mukundinyoza.”
Kapena kuti, “Abale anga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa ana aamuna a mimba yanga,” kutanthauza kuti mimba imene inandibereka (mimba ya mayi anga).
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndapulumuka ndi khungu la mano anga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo simukukhutira ndi mnofu wanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzaimirira pafumbi.”
Kapena kuti, “Impso zanga zasiya kugwira ntchito mʼmimba mwanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa ndili ndi mzimu womvetsa zinthu.”
Kapena kuti, “mtundu wa anthu; Adamu.”
Kapena kuti, “wampatuko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mafupa ake anali amphamvu.”
Apa akunena mphamvu zake.
Kapena kuti, “ndulu ya mamba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Lilime la mphiri lidzamupha.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo sadzachimeza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kodi mzimu wanga ukanakhalabe woleza mtima?”
Kapena kuti, “amakhala amphamvu.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼkanthawi kochepa,” kutanthauza kuti amafa mwamsanga ndipo samva kupweteka.
Kapena kuti, “Malangizo a anthu oipa ndi osiyana; Mapulani a anthu oipa ndi osiyana.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngati miyezi yake itadulidwa pakati.”
Kapena kuti, “amene angaphunzitse Mulungu nzeru.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo mafuta a mʼmafupa ake ali ofewa.”
Kapena kuti, “amafa mtima ukumupweteka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zizindikiro zawo.”
Kapena kuti, “lamʼkhwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo adzakoka anthu onse kuti amutsatire.”
Kapena kuti, “Wamphamvuyonse zimamusangalatsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo umavula zovala za anthu amaliseche.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “misampha ya mbalame.”
Kapena kuti, “amene moyo wawo unathera panjira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtsinje.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa lamiyala.”
Kapena kuti, “Koma wankhope yakugwa.”
Kapena kuti, “ndidandaula moukira.”
Kapena kuti, “kuposa zimene anandiuza kuti ndichite.”
Migula ndi mizera ikuluikulu. Ena amati milambala.
Mabaibulo ena amati, “amagwira ntchito yoyenga mafuta mʼminda ya anthu oipa.”
Kapena kuti, “Moyo wa anthu amene avulala umapempha.”
Mabaibulo ena amati, “Mulungu saimba aliyense mlandu wochita zoipa.”
Kapena kuti, “madzi oundana amene asungunuka.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mimba idzamuiwala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma maso ake ali pa njira zawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalo ake okwezeka.”
Kapena kuti, “woyera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi mpweya (mzimu) umene watuluka mwa iwe ndi wandani?”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Ndipo Abadoni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anatambasula kumpoto.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amaduladula Rahabi.”
Kapena kuti, “mphepo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kulankhula mwandakatulo.”
Kapena kuti, “ndidzapitirizabe.”
Kapena kuti, “sudzandinyoza.”
Kapena kuti, “masiku onse a moyo wanga.”
Kapena kuti, “wampatuko.”
Mabaibulo ena amati, “Ndikuphunzitsani ndi dzanja la Mulungu.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amakhuthulidwa.”
Zikuoneka kuti apa akunena ntchito za mʼmigodi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kulemera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kulankhula mwandakatulo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasiku a unyamata wanga.”
Kapena kuti, “antchito.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkubisala.”
Kapena kuti, “malaya akunja odula manja.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchisa changa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ankadonthera mʼmakutu mwawo pangʼonopangʼono.”
Kapena kuti, “amʼmakhwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akwapulidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwambi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wakhwefula chingwe cha uta wanga.”
Mabaibulo ena amati, “Popanda aliyense wowathandiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mafupa anga amabowoledwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “angamenye mulu wa zinthu zowonongeka.”
Kapena kuti, “amene zinthu sizikuwayendera bwino.”
Mabaibulo ena amati, “chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.”
Kapena kuti, “mbadwa zanga zidzazulidwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “umene ungadye mpaka kuwonongeratu zinthu.”
Kapena kuti, “Ungazule mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akaimilira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmimba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchititsa maso a mkazi wamasiye kufooka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili mʼmimba mwa mayi anga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chiuno chake sichinandidalitse.”
Kapena kuti, “Fupa lapaphewa langa ligwe.”
Kapena kuti, “kuchoka mʼmalomwake; pafupa lakumtunda kwake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinaona kuwala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyama yake.”
Kapena kuti, “Siginecha yanga ndi imeneyi.”
Kapena kuti, “chifukwa ankadziona kuti ndi wolungama.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wamasiku ochepa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Masiku alankhule.”
Kapena kuti, “Si kuchuluka kwa masiku kokha kumene kumapangitsa.”
Kapena kuti, “amene wadzudzula Yobu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mimba yanga ili ngati.”
Kapena kuti, “kupereka dzina laulemu kwa munthu aliyense.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Lilime langa ndi mʼkamwa mwanga zikuyenera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amaika chidindo pa.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “ndi chida.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “moyo wake umaipidwa.”
Kapena kuti, “moyo wake umakana.”
Kapena kuti, “amaonekera.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “mngelo.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “ukhale wathanzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzaimbira.”
Mabaibulo ena amati, “Koma sindinapindule chilichonse.”
Kapena kuti, “Iye wawombola moyo wanga.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “Kuti achotse moyo wake.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼkamwa mumasiyanitsira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inu amuna a mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nʼkutenga mzimu.”
Kapena kuti, “olemekezeka kuposa onyozeka.”
Kapena kuti, “wampatuko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Anthu a mtima.”
Nʼkutheka kuti akunena Mulungu.
Kapena kuti, “samvetsera bodza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mphamvu za mtima wake nʼzazikulu.”
Kapena kuti, “ndi chida.”
Kapena kuti, “ampatuko.”
Kapena kuti, “kuwomba mʼmanja mwanjiru.”
Kapena kuti, “Nʼzosatheka kufufuza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mumsasa wake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuwala kwake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mizu ya nyanja.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amaika chidindo padzanja la munthu aliyense.”
Kapena kuti, “panthaka yachonde yapadziko lapansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngati chikwapu.”
Kapena kuti, “ngati galasi lachitsulo.”
Kumene ndi kuwala kwa dzuwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ali ndi mtima wanzeru.”
Awa ndi mawu okuluwika a Chiheberi onena za angelo omwe ndi ana a Mulungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi mʼmasiku ako unayamba.”
Kapena kuti, “mageti a mthunzi wa imfa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ambiri.”
Mabaibulo ena amati, “chingʼaningʼani chimamwazikana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mazaroti.” Pa 2Mf 23:5, mawu ofanana ndi amenewa, omwe akunena zinthu zambiri, akunena za gulu la nyenyezi la Zodiyaki.
Mabaibulo ena amati, “gulu la nyenyezi la Chimbalangondo Chachikulu.”
Mabaibulo ena amati, “mumtima.”
Mabaibulo ena amati, “Kapena ndi ndani anaika nzeru mʼmaganizo.”
Kapena kuti, “modyeramo ziweto.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amaichititsa kuti iiwale.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Imapita kukakumana ndi zida zankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Imameza nthaka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “padzino la thanthwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Umange nkhope zawo.”
Kapena kuti, “ndidzakuyamikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Behemoti.”
Kapena kuti, “amkuwa.”
Kapena kuti, “yamʼkhwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “msampha.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Leviyatani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “minga.”
Umenewu ndi mpaliro umene mwina unali ndi mano oyangʼana kumbuyo ngati dzino la mbedza.
Kapena kuti, “umangodzigwera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zakumaso kwake.”
Kapena kuti, “mkuwa imangowuona.”
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndithudi ndidzatukula nkhope yake mʼmwamba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yehova anabweza ukapolo wa Yobu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngʼombe 2,000 zimene zinkagwira ntchito zili ziwiriziwiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anamwalira ali wokalamba komanso ali ndi masiku ambiri.”