Rute
1 Tsopano zinachitika kuti, m’masiku amene oweruza+ anali atsogoleri, m’dzikomo munagwa njala.+ Ndiyeno munthu wina anasamuka ku Betelehemu+ wa ku Yuda kukakhala m’dziko la Mowabu+ monga mlendo. Anasamuka ndi mkazi wake ndi ana ake awiri aamuna. 2 Munthuyo dzina lake anali Elimeleki, ndipo mkazi wake anali Naomi. Mayina a ana akewo anali Maloni ndi Kiliyoni. Anthuwa anali a ku Betelehemu Efurata+ wa ku Yuda. Ndipo anafika m’dziko la Mowabu ndi kukhazikika kumeneko.
3 Patapita nthawi, Elimeleki mwamuna wa Naomi anamwalira, moti Naomi anatsala ndi ana ake awiriwo. 4 Kenako, anawo anakwatira akazi achimowabu.+ Wina dzina lake anali Olipa, wina anali Rute.+ Ndipo anakhalabe kumeneko zaka pafupifupi 10. 5 Patapita nthawi, ana awiriwo, Maloni ndi Kiliyoni, nawonso anamwalira, moti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja, komanso wopanda mwamuna. 6 Pamenepo iye limodzi ndi apongozi ake anakonzekera ulendo wochoka kudziko la Mowabu, chifukwa ali kumeneko anamva kuti Yehova wakumbukira anthu ake+ powapatsa chakudya.+
7 Chotero Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kumene anali kukhalako,+ n’kuyamba ulendo wobwerera kudziko la Yuda. 8 Kenako Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.+ 9 Yehova akudalitseni.+ Aliyense apeze mpumulo+ m’nyumba ya mwamuna wake.” Kenako anawapsompsona.+ Pamenepo iwo anayamba kulira mokweza mawu, 10 ndipo anaumirira kuti: “Ayi musatero, ife tipita nanu kwanu.”+ 11 Koma Naomi anati: “Bwererani ana anga. Palibe chifukwa choti tipitire limodzi. Kodi ndingathenso kubereka ana, ndipo kodi anawo angadzakhale amuna anu?+ 12 Bwererani ana anga, pitani, popeza ndakalamba kwambiri moti sindingakwatiwenso. Ngakhale n’tanena kuti ndikwatiwa pofika usiku wa lero n’kubereka ana aamuna,+ 13 kodi mungawadikirirebe mpaka atakula? Kodi mungadzisungebe osakwatiwa powadikirira? Ayi ndithu ana anga, zimene zinakuchitikirani zimandiwawa kwambiri, pakuti dzanja la Yehova landiukira.”+
14 Atatero iwo analiranso mokweza mawu. Kenako Olipa anapsompsona apongozi ake powatsanzika. Koma Rute anawaumirirabe.+ 15 Choncho Naomi anati: “Taona m’bale wako wamasiye wabwerera kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake.+ Bwerera naye limodzi.”+
16 Ndiyeno Rute anati: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni, pakuti kumene inu mupite inenso ndipita komweko, kumene inu mugone inenso ndigona komweko.+ Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga,+ ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.+ 17 Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko,+ ndipo ndidzaikidwanso komweko. Yehova andilange kwambiri+ ngati chinachake kupatulapo imfa chingandilekanitse ndi inu.”
18 Ataona kuti walimbikira zoti apite naye limodzi,+ anasiya kumuuza kuti abwerere. 19 Ndipo anapitiriza ulendo wawo mpaka anafika ku Betelehemu.+ Atangofika ku Betelehemu, anthu mumzinda wonsewo anayamba kulankhula za iwo.+ Akazi anali kufunsa kuti: “Kodi si Naomi+ uyu?” 20 Koma iye powayankha anali kunena kuti: “Musanditchulenso kuti Naomi,* muzinditchula kuti Mara,* chifukwa Wamphamvuyonse+ wachititsa moyo wanga kukhala wowawa kwambiri.+ 21 Ndinali ndi zonse pochoka kuno,+ koma Yehova wandibweza wopanda kanthu.+ Munditchuliranji kuti Naomi, pamene ndi Yehova amene wandichititsa kukhala wonyozeka,+ ndipo ndi Wamphamvuyonseyo amene wandigwetsera tsokali?”+
22 Umu ndi mmene Naomi anabwererera kwawo. Anabwerera ndi Rute mkazi wachimowabu, mpongozi wake, kuchokera kudziko la Mowabu.+ Iwo anafika ku Betelehemu+ kumayambiriro kwa nyengo yokolola balere.+
2 Panali munthu wina wolemera kwambiri+ yemwe anali wachibale+ wa mwamuna wake wa Naomi. Dzina lake anali Boazi,+ wa kubanja la Elimeleki.
2 Tsiku lina Rute mkazi wachimowabu uja anapempha Naomi kuti: “Chonde ndiloleni ndipite kuminda ndikakunkhe+ balere m’mbuyo mwa aliyense amene angandikomere mtima.” Ndipo Naomi anamuyankha kuti: “Pita mwana wanga.” 3 Pamenepo Rute ananyamuka n’kupita, ndipo anakalowa m’munda wina ndi kuyamba kukunkha m’mbuyo mwa okolola.+ Mwamwayi mundawo unali wa Boazi,+ wa ku banja la Elimeleki.+ 4 Kenako Boazi anafika kuchokera ku Betelehemu ndipo anauza okololawo kuti: “Yehova akhale nanu.”+ Iwo anayankha mwa nthawi zonse kuti: “Yehova akudalitseni.”+
5 Pamenepo Boazi+ anafunsa mnyamata amene anamuika kukhala kapitawo kuti: “Nanga kodi mtsikana uyu ndi wochokera ku banja liti?” 6 Kapitawoyo anayankha kuti: “Mtsikana ameneyu ndi Mmowabu+ amene anabwera limodzi ndi Naomi kuchokera ku Mowabu.+ 7 Iyeyu atafika anapempha kuti, ‘Chonde ndikunkheko.+ Ndizitola balere wotsala m’mbuyo mwa okololawo.’ Atatero, analowa m’mundamu n’kuyamba kukunkha. Wakhala akukunkha kuyambira m’mawa mpaka posachedwapa pamene anakhala pansi pang’ono m’chisimbamu.”*+
8 Kenako Boazi anauza Rute kuti: “Tamvera mwana wanga, usapitenso kumunda wina kukakunkha.+ Usachoke pano kupita kwina, ukhale pafupi ndi atsikana anga antchitowa.+ 9 Maso ako akhale pamunda umene akukolola, ndipo uzipita nawo limodzi kumeneko. Anyamatawa ndawalamula kuti asakukhudze.+ Ukamva ludzu, nawenso uzipita kumitsuko kukamwa madzi amene anyamatawa azitunga.”+
10 Atamva zimenezo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ n’kunena kuti: “Zatheka bwanji kuti mundiganizire ndi kundikomera mtima chotere, ine wokhala mlendo?”+ 11 Ndiyeno Boazi anamuyankha kuti: “Ndamva zonse zimene wachitira apongozi ako chimwalilireni mwamuna wako.+ Ndamvanso kuti unasiya bambo ako ndi mayi ako, komanso dziko la abale ako, n’kubwera kuno kwa anthu amene sunali kuwadziwa n’kale lonse.+ 12 Yehova akudalitse chifukwa cha zimene wachita,+ ndipo Yehova, Mulungu wa Isiraeli akufupe mokwanira.+ Iye amene m’mapiko mwake wathawiramo ndi kupezamo chitetezo.”+ 13 Atamva zimenezi Rute anati: “Mwandikomera mtima mbuyanga. Mwanditonthoza mtima, komanso mwalankhula mondilimbitsa mtima+ ngati kuti ndine mtsikana wanu wantchito pamene sindili mmodzi wa atsikana anu antchito.”+
14 Ndipo pa nthawi ya chakudya Boazi anaitana Rute kuti: “Tabwera kuno udzadye mkate+ ndiponso uziusunsa mu vinyo wowawasayu.” Choncho Rute anadzakhala pansi limodzi ndi okololawo, ndipo Boazi anali kum’patsira mbewu zokazinga,+ iye n’kumadya moti anakhuta mpaka zina kutsala. 15 Atatha kudya ananyamuka kukayambanso kukunkha.+ Tsopano Boazi analamula anyamata ake kuti: “Muloleni akunkhe pomwe mwadula kale balere, ndipo musam’vutitse.+ 16 Komanso, muzisololapo balere wina pamitolopo n’kumamusiya pansi kuti iye akunkhe.+ Ndipo musamuletse.”
17 Choncho Rute anapitiriza kukunkha m’mundamo kufikira madzulo.+ Atamaliza anapuntha+ balere amene anakunkhayo moti anakwana pafupifupi muyezo umodzi wa efa.*+ 18 Kenako ananyamula balereyo ndi kubwerera kumzinda, ndipo apongozi ake anaona balere amene anakunkhayo. Pambuyo pake, Rute anatenga chakudya chimene chinatsalako+ atakhuta chija n’kupatsa apongozi ake.
19 Tsopano apongozi ake anam’funsa kuti: “Kodi unakakunkha kuti lero? Adalitsike amene wakuganizirayo.”+ Ndiyeno iye anauza apongozi akewo za mwinimunda umene anakakunkhamo, kuti: “Dzina la mwinimunda umene ndakunkhamo lero ndi Boazi.” 20 Pamenepo Naomi anauza mpongozi wakeyo kuti: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa amoyo ndi akufa,+ am’dalitse munthu ameneyu.”+ Ndipo Naomi anapitiriza kuti: “Munthuyutu ndi wachibale wathu.+ Ndi mmodzi wa otiwombola.”+ 21 Ndiyeno Rute mkazi wachimowabuyo anati: “Moti anandiuzanso kuti, ‘Usachoke, uzikhala pafupi ndi antchito angawa mpaka adzamalize kundikololera zonse.’”+ 22 Ndipo Naomi+ anauza Rute mpongozi wake+ kuti: “Ndi bwinodi mwana wanga, uzipita limodzi ndi atsikana akewo, kuopera kuti angakakunyoze ukapita kumunda wina.”+
23 Choncho Rute anapitiriza kukhala pafupi ndi atsikana antchito a Boazi, mpaka pamene anamaliza kukolola balere+ ndi tirigu. Ndipo anapitiriza kukhala ndi apongozi ake.+
3 Tsopano Naomi, apongozi a Rute, anamuuza kuti: “Mwana wanga, kodi sindiyenera kukupezera mpumulo,+ kuti zikuyendere bwino? 2 Wakhala ukukunkha pambuyo pa atsikana antchito a Boazi. Kodi iye si wachibale wathu?+ Pajatu usiku walero akhala akupeta+ balere pamalo ake opunthira. 3 Choncho samba ndi kudzola mafuta+ ndi kuvala zovala+ ndipo upite kopunthirako. Koma iye asakuzindikire mpaka atamaliza kudya ndi kumwa. 4 Ndiyeno pamene akugona, ukaone kuti wagona pati. Ukapite pamene wagonapo ndi kuvundukula kumapazi ake ndi kugona pomwepo. Ndipo iye adzakuuza zoti uchite.”
5 Pamenepo Rute anamuyankha Naomi kuti: “Zonse zimene mwanena ndikachita.” 6 Ndipo anapita kopunthirako n’kuchita zonse zimene apongozi ake anamuuza. 7 Boazi anadya ndi kumwa, ndipo anali wosangalala mumtima mwake.+ Kenako anapita kukagona chakumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndi kuvundukula kumapazi kwa Boazi n’kugona. 8 Ndiye pakati pa usiku Boazi anayamba kunjenjemera. Chotero anadzuka n’kukhala tsonga. Koma anadabwa kuona mkazi atagona kumapazi ake! 9 Pamenepo anafunsa kuti: “Ndiwe yani?” Poyankha, Rute anati: “Ndine Rute kapolo wanu. Mufunditse kapolo wanu chovala chanu, pakuti ndinu wotiwombola.”+ 10 Atatero, Boazi anati: “Yehova akudalitse,+ mwana wanga. Kukoma mtima kosatha+ kumene wasonyeza panopa kukuposa koyamba kuja,+ popeza sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemera. 11 Tsopano usachite mantha mwana wanga. Ndidzakuchitira zonse zimene wanena,+ chifukwa aliyense mumzinda wathu akudziwa kuti ndiwe mkazi wabwino kwambiri.+ 12 Komano ngakhale kuti ndinedi wokuwombolani,+ pali wachibale wina wapafupi kwambiri kuposa ine+ amene angakuwombole. 13 Gona pompano lero. Ngati iye angakuwombole+ mawa, zili bwino! Akuwombole. Koma ngati sakufuna kukuwombola, ineyo ndidzakuwombola. Ndithudi, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ndidzakuwombola. Gona kufikira m’mawa.”
14 Choncho anagonabe kumapazi a Boazi kufikira m’mawa, kenako anadzuka kudakali mdima. Boazi sanafune kuti anthu adziwe kuti kopunthira mbewuko kunafika mkazi.+ 15 Ndiyeno anamuuza kuti: “Bwera nayo kuno nsalu wafundayo, uitambasule.” Iye anaitambasula, ndipo Boazi anathirapo miyezo 6* ya balere ndi kum’senza pamutu. Zitatero, Boazi analowa mumzinda.
16 Tsopano Rute anabwerera kwa apongozi ake, ndipo anam’funsa kuti: “Ndiwe yani, mwana wanga?” Pamenepo anawafotokozera zonse zimene Boazi anam’chitira. 17 Anafotokozanso kuti: “Wandipatsa balere uyu, wokwana miyezo 6, n’kundiuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’”+ 18 Atatero, Naomi anayankha kuti: “Dekha, mwana wanga, kufikira utadziwa mmene nkhaniyi ithere. Chifukwa iye sakhala pansi mpaka ataithetsa nkhaniyi lero.”+
4 Zitatero, Boazi anapita kuchipata.+ Kumeneko iye anakhala pansi. Ali chikhalire choncho, anaona wowombola anam’tchula uja+ akudutsa. Ndiyeno Boazi anati: “Iwe Uje takhotera pano, khala pansi apa.” Motero anakhota n’kukhala pansi. 2 Kenako anatenga amuna 10 mwa akulu+ a mzindawo n’kuwauza kuti: “Khalani pansi.” Iwo anakhaladi pansi.
3 Ndiyeno Boazi anauza wowombola+ uja kuti: “Naomi amene wabwerera kuchokera kudziko la Mowabu+ ayenera kugulitsa munda umene unali wa m’bale wathu Elimeleki.+ 4 Ndiye ine ndaganiza zoti ndikuuze kuti, ‘Ugule mundawo+ pamaso pa anthu ndi pamaso pa akulu a mzinda uno.+ Ngati ukufuna kuuwombola, uwombole. Koma ngati sukufuna undiuze kuti ndidziwe, popeza palibenso wina amene angauwombole koma iweyo,+ pambuyo pako pali ine.’” Pamenepo, wowombola uja anati: “Ndiuwombola ineyo.”+ 5 Kenako Boazi anati: “Ukadzagula mundawo kwa Naomi, ndiye kuti waugulanso kwa Rute Mmowabu, amene mwamuna wake anamwalira, kuti dzina la mwamuna wakeyo libwerere pacholowa chake.”+ 6 Poyankha wowombolayo anati: “Sinditha kuuwombola, kuopera kuti ndingawononge cholowa changa. Iweyo uuwombole m’malo mwa ine, chifukwa ine sinditha kuuwombola.”
7 Tsopano, kale mu Isiraeli munali mwambo wokhudza ufulu wowombola ndiponso wokhudza kusinthana ufuluwo, pofuna kuti atsimikizirane chilichonse. Mwambo wake unali wotere: Munthu anali kuvula nsapato+ yake ndi kuipereka kwa mnzake. Uwu ndiwo unali umboni wotsimikizirana mu Isiraeli. 8 Choncho pamene wowombola uja anauza Boazi kuti: “Ugule iweyo,” wowombolayo anavula nsapato yake.+ 9 Kenako Boazi anauza akulu ndi anthu onse kuti: “Inu ndinu mboni+ lero kuti ndikugula kwa Naomi zonse zimene zinali za Elimeleki, ndi zonse zimene zinali za Kiliyoni ndi Maloni. 10 Komanso ndikugula Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni, kukhala mkazi wanga kuti dzina la mwamuna wake amene anamwalira+ libwerere pacholowa chake, kutinso lisafafanizike pakati pa abale ake ndi mumzinda wathu. Inu ndinu mboni+ lero.”
11 Pamenepo anthu onse ndi akulu amene anali pachipata anayankha kuti: “Ndife mboni! Yehova adalitse mkazi amene akulowa m’nyumba mwako kuti akhale ngati Rakele+ ndi Leya,+ akazi amene anabereka ana a nyumba ya Isiraeli.+ Uonetse kulemekezeka kwako mu Efurata+ ndi kudzipangira dzina m’Betelehemu.+ 12 Ndipo kudzera mwa ana amene Yehova adzakupatsa kwa mtsikanayu,+ nyumba yako ikhale ngati nyumba ya Perezi, amene Tamara anaberekera Yuda.”+
13 Choncho Boazi anatenga Rute kukhala mkazi wake ndipo anagona naye. Pamenepo Yehova anam’dalitsa ndipo anatenga pakati+ n’kubereka mwana wamwamuna. 14 Zitatero akazi anayamba kuuza+ Naomi kuti: “Adalitsike Yehova,+ amene wachititsa kuti usasowe wokuwombola lero, kuti dzina lake lifalitsidwe mu Isiraeli. 15 Mwanayu watsitsimutsa moyo wako ndipo adzakusamalira mu ukalamba wako,+ chifukwa wabadwa kwa mpongozi wako amene amakukonda,+ amenenso ndi woposa ana aamuna 7.”+ 16 Choncho Naomi ananyamula mwanayo, ndipo anakhala mlezi wake. 17 Pamenepo akazi okhala naye pafupi+ anatcha mwanayo dzina lakuti Obedi.+ Ndipo iwo anati: “Mwana wabadwa kwa Naomi.” Obedi ndiye bambo ake a Jese,+ bambo ake a Davide.
18 Tsopano uwu ndiwo mzere wa mbadwa za Perezi:+ Perezi anabereka Hezironi,+ 19 Hezironi anabereka Ramu, Ramu+ anabereka Aminadabu, 20 Aminadabu+ anabereka Naasoni,+ Naasoni anabereka Salimoni, 21 Salimoni+ anabereka Boazi, Boazi+ anabereka Obedi, 22 Obedi anabereka Jese,+ ndipo Jese anabereka Davide.+
Dzina lakuti “Naomi” limatanthauza “Kusangalatsa Kwanga.”
Dzina lakuti “Mara” limatanthauza “Kuwawa.”
Kanyumba ka kumunda. Mawu ena, “khumbi” kapena “dindiro.”
“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
Malinga ndi mabuku a Arabi, imeneyi inali miyezo 6 ya seya kapena kuti malita 44. Zikuoneka kuti zimenezi ndizo akanakwanitsa kusenza pamutu.