Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 1 Samuel 1:1-31:13
  • 1 Samueli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 Samueli
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Samueli

Samueli* Woyamba

kapena, malinga ndi Baibulo lachigiriki la Septuagint, MAFUMU WOYAMBA

1 Tsopano panali mwamuna wina wa ku Ramatayimu-zofimu,+ kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Elikana.+ Iye anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufi+ Mwefuraimu.* 2 Elikana anali ndi akazi awiri. Mkazi wina dzina lake anali Hana ndipo wina anali Penina. Penina anabereka ana koma Hana analibe ana.+ 3 Chaka ndi chaka mwamuna ameneyu anali kutuluka mumzinda wake n’kupita ku Silo,+ kukagwada ndi kuweramira pansi+ pamaso pa Yehova wa makamu ndi kupereka nsembe zake. Kumeneko n’kumene ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinihasi,+ anali kutumikira monga ansembe a Yehova.+

4 Ndiyeno tsiku lina Elikana anali kupereka nsembe, ndipo anapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi,+ 5 koma Hana anangom’patsa gawo limodzi. Komabe, iye anali kukonda kwambiri Hana+ ngakhale kuti Yehova anali atatseka mimba yake.+ 6 Mkazi mnzake wa Hana anali kum’sautsa+ kwambiri n’cholinga choti amukhumudwitse, chifukwa chakuti Yehova anali atatseka mimba yake. 7 Chaka ndi chaka+ iye anali kuchita zimenezi nthawi zonse akapita kunyumba ya Yehova.+ Umu ndi mmene Penina anali kusautsira Hana, moti Hana anali kulira ndiponso sankadya. 8 Ndiyeno Elikana mwamuna wake anati: “Hana, n’chifukwa chiyani ukulira, ndipo n’chifukwa chiyani sukudya? Komanso n’chifukwa chiyani ukupwetekedwa mtima?+ Kodi sindine woposa ana aamuna 10 kwa iwe?”+

9 Pamenepo Hana anaimirira atadya ndi kumwa ku Silo. Apa n’kuti Eli wansembe atakhala pampando, pakhomo la kachisi+ wa Yehova. 10 Hana anali wokhumudwa kwabasi,+ ndipo anayamba kupemphera kwa Yehova+ ndi kulira kwambiri.+ 11 Iye anayamba kulonjeza+ kuti: “Inu Yehova wa makamu, mukaona nsautso yanga, ine kapolo wanu wamkazi,+ ndi kundikumbukira,+ ndiponso ngati simudzaiwala kapolo wanu wamkazi ndi kum’patsa mwana wamwamuna, ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo lezala silidzadutsa m’mutu mwake.”+

12 Pamene anali kupemphera choncho kwa Yehova kwa nthawi yaitali,+ Eli anali kuyang’anitsitsa pakamwa pake. 13 Koma Hana anali kulankhula mumtima mwake.+ Milomo yake inali kugwedera koma sanali kutulutsa mawu. Eli ataona zimenezo anaganiza kuti waledzera.+ 14 Choncho Eli anamuuza kuti: “Kodi ukhala woledzera mpaka liti?+ Pita kaye, kuledzera kwakoku kuyambe kwatha.” 15 Pamenepo Hana anayankha kuti: “Ayi mbuyanga! Ine ndine mkazi wopsinjika maganizo. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa ayi, koma ndikufotokoza nkhawa zanga zonse kwa Yehova.+ 16 Musachititse kapolo wanu wamkazi kukhala ngati mkazi wopanda pake,+ popeza ndikulankhulabe mpaka pano chifukwa cha kuchuluka kwa nkhawa ndi nsautso.”+ 17 Pamenepo Eli anamuyankha kuti: “Pita mu mtendere,+ ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse zimene wam’pempha.”+ 18 Poyankha anati: “Pitirizani kundikomera mtima ine kapolo wanu.”+ Ndiyeno mkaziyo anachoka ndi kupita kukadya,+ ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.+

19 Kenako anadzuka m’mawa kwambiri n’kugwada ndi kuwerama mpaka nkhope zawo pansi pamaso pa Yehova. Atatero anabwerera kunyumba kwawo ku Rama.+ Ndiyeno Elikana anagona+ ndi mkazi wake Hana, ndipo Yehova anayamba kum’kumbukira.+ 20 Pamene chaka chinkatha, Hana anatenga pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna n’kumutcha dzina lake+ Samueli,* chifukwa anati, “ndinam’pempha+ kwa Yehova.”

21 Patapita nthawi, mwamunayu Elikana anapita pamodzi ndi banja lake lonse kukapereka kwa Yehova nsembe ya pachaka+ ndi nsembe yake yalonjezo.+ 22 Koma Hana sanapite nawo,+ pakuti anali atauza mwamuna wake kuti: “Mwanayu akangosiya kuyamwa,+ ndiyenera kupita naye kuti akaonekere pamaso pa Yehova ndi kukhala kumeneko mpaka kalekale.”*+ 23 Pamenepo Elikana mwamuna wake+ anamuuza kuti: “Chita zimene ukuona kuti n’zabwino kwa iwe.+ Ukhale pakhomo kufikira mwanayo atasiya kuyamwa, ndipo Yehova akwaniritse mawu ake.”+ Choncho mkaziyo anakhalabe pakhomo ndipo anapitiriza kulera mwana wake kufikira atasiya kuyamwa.+

24 Mwanayo atangosiya kuyamwa, Hana anapita naye ku Silo atatenga ng’ombe yaing’ono yamphongo yazaka zitatu, ufa wokwana muyezo umodzi wa efa* ndi mtsuko waukulu wa vinyo.+ Iye analowa m’nyumba ya Yehova ku Silo,+ ndipo mwanayo anali naye limodzi. 25 Kenako anapha ng’ombe yaing’ono yamphongoyo ndipo anabweretsa mwana wake wamwamunayo kwa Eli.+ 26 Pamenepo Hana anati: “Pepani mbuyanga! Pali moyo wanu+ mbuyanga, ine ndine mkazi amene ndinaima ndi inu pamalo ano n’kupemphera kwa Yehova.+ 27 Ndinali kupemphera kuti Yehova andipatse mwana uyu, kuti andipatse+ chimene ndinam’pempha.+ 28 Ndipo ine ndikum’pereka* kwa Yehova.+ Ndam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.”

Pamenepo iye* anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa Yehova.+

2 Ndiyeno Hana anayamba kupemphera+ kuti:

“Mtima wanga ukukondwera mwa Yehova,+

Nyanga* yanga yakwezekadi kudzera mwa Yehova.+

Ndikutsutsana ndi adani anga molimba mtima,

Pakuti ndikukondwera ndi chipulumutso chochokera kwa inu.+

 2 Palibe woyera ngati Yehova. Palibe aliyense koma inu nokha.+

Palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.+

 3 Musalankhule modzikweza kwambiri anthu inu,

Pakamwa panu pasatuluke mawu odzikuza,+

Pakuti Yehova ndi Mulungu wodziwa zonse.+

Ndipo zochita za anthu, iye amaziyeza molondola.+

 4 Oponya mivi ndi uta mwaluso agwidwa ndi mantha,+

Koma olefuka apeza mphamvu zochuluka.+

 5 Amene anali okhuta ayenera kugwira ganyu kuti apeze chakudya,+

Koma anjala, njala yawo yawathera.+

Ngakhale wosabereka, wabereka ana 7,+

Koma amene anali ndi ana aamuna ambiri, wasiya kubereka.+

 6 Yehova ndi Wakupha ndi Wosunga moyo,+

Iye ndi Wotsitsira Kumanda,+ ndiponso Woukitsa.+

 7 Yehova ndi Wopereka Umphawi+ ndi Wolemeretsa,+

Wotsitsa ndiponso Wokweza,+

 8 Iye amadzutsa wonyozeka, kumuchotsa pafumbi.+

Amachotsa osauka padzala,+

Kuti awakhazike pakati pa anthu olemekezeka,+ ndipo amawapatsa mpando wachifumu waulemerero.+

Pakuti michirikizo ya dziko lapansi ndi ya Yehova,+

Ndipo anakhazika dziko lapansi pamichirikizo imeneyo.

 9 Mapazi a okhulupirika ake amawateteza.+

Koma anthu oipa amawawononga mu mdima,+

Pakuti munthu sakhala wapamwamba chifukwa cha mphamvu zake.+

10 Onse olimbana ndi Yehova adzagwidwa ndi mantha.+

Motsutsana nawo, iye adzagunda ngati mabingu kumwamba.+

Yehova mwiniwake adzaweruza dziko lonse lapansi,+

Kuti apereke mphamvu kwa mfumu yake,+

Ndi kuti akweze nyanga ya wodzozedwa wake.”+

11 Kenako Elikana anapita kunyumba kwake ku Rama, koma mwanayo anakhala mtumiki+ wa Yehova pamaso pa wansembe Eli.

12 Tsopano ana aamuna a Eli anali anthu opanda pake.+ Iwo anali kunyalanyaza Yehova.+ 13 Munthu aliyense akamapereka nsembe ankayeneranso kupereka gawo la nyamayo kwa wansembe.+ Ndiyeno zimene zinali kuchitika n’zakuti, pamene nyama imeneyi inali kuwira, mtumiki wa wansembe anali kubwera ndi foloko ya mano atatu m’manja mwake.+ 14 Akatero anali kupisa mumphika kapena chophikira cha zigwiriro ziwiri, munkhali, kapena m’chophikira cha chigwiriro chimodzi. Ndipo wansembe anali kutenga chilichonse chimene folokoyo yatulutsa. Umu ndi mmene anali kuchitira ku Silo, kwa Aisiraeli onse opita kumeneko.+ 15 Komanso, asanapsereze mafuta,+ mtumiki wa wansembe anali kubwera kudzauza munthu wopereka nsembeyo kuti: “Ndipatse nyama yaiwisi kuti ndikamuwotchere wansembe, kuti wansembe asalandire nyama yophika koma yaiwisi.”+ 16 Wopereka nsembeyo akanena kuti: “Yembekeza kaye apsereze mafutawo,+ kenako utenge chilichonse chimene mtima wako ukufuna,”+ iye anali kuyankha kuti: “Ayi, ndipatse pompano, ukapanda kundipatsa, ndichita kulanda!”+ 17 Tchimo la atumikiwa linakula kwambiri pamaso pa Yehova,+ chifukwa amuna amenewa sanali kulemekeza nsembe ya Yehova.+

18 Ndiyeno Samueli anali kutumikira+ pamaso pa Yehova, ali mwana ndipo anali kuvala efodi wansalu.+ 19 Komanso chaka ndi chaka mayi ake anali kumusokera kamalaya kakunja kodula manja. Iwo anali kumubweretsera kamalayako akabwera ndi mwamuna wawo kudzapereka nsembe ya pachaka.+ 20 Ndiyeno Eli anadalitsa+ Elikana ndi mkazi wake, ndipo anati: “Yehova akupatsenso mwana kudzera mwa mkazi uyu kulowa m’malo mwa amene anam’pereka kwa Yehova.”+ Kenako makolowo anabwerera kwawo, 21 ndipo Yehova anakomera mtima Hana,+ moti anayamba kutenga pakati ndipo anabereka ana aamuna atatu ndi aakazi awiri.+ Mwanayo Samueli anapitiriza kukula, akukondedwa ndi Yehova.+

22 Ndiyeno Eli anali wokalamba kwambiri ndipo anamva+ zonse zimene ana ake anali kuchitira+ Aisiraeli onse, komanso anamva kuti anali kugona ndi akazi+ otumikira pakhomo la chihema chokumanako.+ 23 Ndipo iye anali kuwauza kuti:+ “Mukuchitiranji zinthu zoterezi?+ Chifukwatu anthu onse akundiuza zinthu zoipa zokhazokha zokhudza inu.+ 24 Musatero+ ana anga, chifukwa nkhani imene ndikumva, imene anthu a Yehova akufalitsa, si yabwino ayi.+ 25 Munthu akachimwira mnzake,+ Mulungu adzam’pepesera,+ koma kodi akachimwira Yehova,+ angamupempherere ndani?”+ Koma anawo sanali kumvera bambo awo+ chifukwa tsopano Yehova anali atatsimikiza mtima kuti awaphe.+ 26 Izi zili choncho, mwanayo Samueli anali kukula ndi kukondedwa kwambiri ndi Yehova komanso anthu.+

27 Ndiyeno munthu wa Mulungu+ anapita kwa Eli ndi kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kodi ine sindinadzisonyeze kunyumba ya kholo lako pamene anali akapolo kunyumba ya Farao ku Iguputo?+ 28 Kholo lakolo ndinalisankha kuchokera m’mafuko onse a Isiraeli kuti akhale wansembe wanga,+ ndipo azikwera paguwa langa lansembe+ kuti utsi wa nsembezo uzikwera kumwamba, kutinso azivala efodi pamaso panga. Ndinachita izi kuti ndipatse nyumba ya kholo lako nsembe zonse zotentha ndi moto za ana a Isiraeli.+ 29 N’chifukwa chiyani anthu inu mukunyozabe nsembe zanga+ zimene ndinalamula m’nyumba yanga,+ n’kumalemekezabe ana anu koposa ine mwa kudzinenepetsa+ ndi mbali yabwino kwambiri ya nsembe iliyonse ya anthu anga Aisiraeli?+

30 “‘N’chifukwa chake Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ndinanenadi kuti, A m’nyumba yako ndiponso a m’nyumba ya kholo lako adzanditumikira mpaka kalekale.”+ Koma tsopano Yehova akuti: “Sindingachitenso zimenezo, chifukwa amene akundilemekeza+ ndiwalemekeza,+ koma amene akundinyoza ndi opanda pake kwa ine.”+ 31 Tsopano imva izi, masiku adzafika pamene ndidzadula dzanja lako ndi la nyumba ya kholo lako, moti m’nyumba yako simudzakhala munthu wokalamba.+ 32 Ndipo m’nyumba yanga udzangoona mdani pakati pa zinthu zonse zabwino zimene zidzachitikira Isiraeli.+ M’nyumba yako simudzapezeka munthu wokalamba. 33 Koma pali munthu wa m’nyumba yako amene sindidzamuchotsa paguwa langa lansembe kuti achititse maso ako mdima ndi kukufooketsa. Ngakhale zili choncho, ochuluka a m’nyumba yako, anthu adzawapha ndi lupanga.+ 34 Ndipo chizindikiro chako chimene chidzachitikira ana ako awiri Hofeni ndi Pinihasi+ ndi ichi: Onse awiri adzafa tsiku limodzi.+ 35 Pamenepo ndidzadziutsira wansembe wokhulupirika+ amene adzachita mogwirizana ndi zimene zili mumtima mwanga ndi zofuna zanga. Ndidzam’mangira nyumba* yokhalitsa, ndipo adzatumikira wodzozedwa wanga+ monga wansembe nthawi zonse. 36 Ndiyeno aliyense wotsala+ m’nyumba yako adzafika ndi kumugwadira kuti alandire ndalama za malipiro ndi mtanda wobulungira wa mkate, ndipo adzati: “Ndiloleni chonde ndigwire ntchito monga wansembe kuti ndipezeko kachakudya.”’”+

3 Zili choncho, mwanayo Samueli anali kutumikira+ Yehova pamaso pa Eli, ndipo mawu a Yehova+ anali osowa masiku amenewo,+ moti masomphenya sanali kuonekaoneka.+

2 Ndiyeno tsiku lina Eli anali atagona m’chipinda chake. Pa nthawiyi, maso ake anali atayamba kuchita mdima+ moti sanali kuona. 3 Nyale ya Mulungu inali isanazimitsidwe, ndipo Samueli anali atagona m’kachisi+ wa Yehova, mmene munali likasa la Mulungu. 4 Ndiyeno Yehova anayamba kuitana Samueli. Ndipo Samueli anayankha kuti: “Ine mbuyanga.”+ 5 Pamenepo anathamangira kwa Eli, n’kunena kuti: “Ndabwera mbuyanga, ndamva kuitana.” Koma Eli anamuuza kuti: “Sindinakuitane. Pita ukagone.” Choncho Samueli anapita kukagonanso. 6 Ndiyeno Yehova anamuitananso, kuti: “Samueli!”+ Pamenepo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli, n’kunena kuti: “Ndabwera mbuyanga, chifukwa ndamva kuitana ndithu.” Koma Eli anamuuza kuti: “Sindinakuitane mwana wanga.+ Pita ukagone.” 7 (Pa nthawiyi Samueli anali asanadziwe Yehova, ndipo anali asanayambe kulandira mawu a Yehova.)+ 8 Ndiyeno Yehova anaitananso kachitatu kuti: “Samueli!” Pamenepo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli, n’kunenanso kuti: “Ndabwera, chifukwa mwandiitana ndithu.”

Atatero, Eli anazindikira kuti Yehova ndi amene anali kuitana mwanayo. 9 Chotero Eli anauza Samueli kuti: “Pita ukagone, ndipo akakuitananso unene kuti, ‘Lankhulani Yehova, chifukwa ine mtumiki wanu ndikumvetsera.’” Choncho Samueli anapita kukagona m’chipinda chake.

10 Kenako Yehova anabwera ndi kuima pamalopo n’kuitananso ngati poyamba paja, kuti: “Samueli, Samueli!” Poyankha Samueli anati: “Lankhulani, ine mtumiki wanu ndikumvetsera.”+ 11 Pamenepo Yehova anayamba kuuza Samueli kuti: “Tamvera! Ndichita+ zinazake mu Isiraeli zoti munthu aliyense akadzamva m’makutu ake onse mudzalira!+ 12 Tsiku limenelo ndidzachitira Eli zonse zimene ndinanena, zoyambirira mpaka zomalizira, zokhudza nyumba yake.+ 13 Umuuze kuti ndidzaweruza nyumba yake+ mpaka kalekale chifukwa cha cholakwa ichi: Iye akudziwa+ kuti ana ake akunyoza Mulungu+ koma sakuwadzudzula.+ 14 N’chifukwa chake ndalumbirira a m’nyumba ya Eli kuti mpaka kalekale sadzapewa chilango chifukwa cha cholakwa cha anthu a m’nyumba yakewo, ngakhale atapereka nsembe.”+

15 Ndiyeno Samueli anagonabe mpaka m’mawa. Atadzuka anatsegula zitseko za nyumba ya Yehova,+ koma anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.+ 16 Tsopano Eli anaitana Samueli, n’kunena kuti: “Samueli, mwana wanga!” Ndipo iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga.” 17 Ndiyeno Eli anamuuza kuti: “Kodi Mulungu wakuuza chiyani? Chonde usandibisire ayi.+ Mulungu akulange ndi kuwonjezerapo,+ ukandibisira ngakhale mawu amodzi pa mawu onse amene iye wakuuza.” 18 Choncho Samueli anamuuza mawu onse ndipo sanam’bisire kanthu. Pamenepo Eli anati: “Ndi Yehova amene wanena. Achite zimene akuona kuti n’zabwino.”+

19 Samueli anapitiriza kukula ndipo Yehova anali naye,+ moti palibe mawu ake alionse amene anapita padera.+ 20 Tsopano Aisiraeli onse kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba,+ anadziwa kuti Samueli ndiye anali wovomerezeka kukhala mneneri wa Yehova.+ 21 Ndipo Yehova anaonekeranso+ ku Silo, pakuti n’kumene Yehova anadzisonyeza kwa Samueli mwa mawu a Yehova.+

4 Samueli anapitiriza kulankhula ndi Aisiraeli onse.

Tsopano Aisiraeli anapita kukamenyana ndi Afilisiti. Choncho anamanga msasa pafupi ndi Ebenezeri,+ ndipo Afilisiti nawonso anamanga msasa ku Afeki.+ 2 Afilisitiwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo+ kuti amenyane ndi Aisiraeli. Nkhondoyo sinawayendere bwino Aisiraeli, moti anagonjetsedwa ndi Afilisiti.+ Iwo anakantha amuna achiisiraeli pafupifupi 4,000 nkhondoyo ili mkati. 3 Ndiyeno anthuwo atabwerera kumsasa, akulu a Isiraeli anayamba kunena kuti: “N’chifukwa chiyani lero Yehova watigonjetsa pamaso pa Afilisiti?+ Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova+ ku Silo, kuti likhale pakati pathu ndi kutipulumutsa m’manja mwa adani athu.” 4 Motero anthuwo anatumiza anthu ku Silo kukatenga likasa la pangano la Yehova wa makamu, amene akukhala pa akerubi.+ Ndipo Hofeni ndi Pinihasi, ana awiri a Eli, anali pamenepo ndi likasa la pangano la Mulungu woona.+

5 Likasa la pangano la Yehova litafika mumsasa, Aisiraeli onse anafuula mokweza kwambiri,+ moti kunali chisokonezo m’dziko lonse. 6 Nawonso Afilisiti anamva phokoso la kukuwa, ndipo anayamba kufunsa kuti: “Kodi phokoso+ limeneli mumsasa wa Aheberi likutanthauza chiyani?” Pamapeto pake, anamva kuti likasa la Yehova labwera mumsasawo. 7 Pamenepo Afilisitiwo anachita mantha, ndipo anati: “Mulungu wafika mumsasa wawo!”+ Ndiyeno anati: “Tsoka latigwera, pakuti zinthu zotere sizinachitikepo ndi kale lonse! 8 Tsoka ife! Adzatipulumutsa ndani m’manja mwa Mulungu wamkuluyu? Ameneyu ndi Mulungu amene anakantha Iguputo ndi masautso amtundu uliwonse m’chipululu.+ 9 Limbani mtima ndi kuchita chamuna Afilisitinu, kuti musatumikire Aheberi ngati mmene iwo akutumikirirani.+ Chitani chamuna ndi kumenya nkhondo!” 10 Chotero Afilisiti anamenyadi nkhondo, ndipo Aisiraeli anagonja+ moti aliyense wa iwo anayamba kuthawira kuhema wake.+ Ndipo amene anaphedwa anali ochuluka kwambiri.+ Panaphedwa amuna oyenda pansi a Isiraeli okwanira 30,000.+ 11 Ngakhalenso likasa la Mulungu linalandidwa,+ ndipo Hofeni ndi Pinihasi, ana awiri a Eli, anafa.+

12 Tsopano mwamuna wina wa fuko la Benjamini anathamanga kuchoka kumalo ankhondowo kukafika ku Silo tsiku limenelo, atang’amba zovala zake+ ndi kudzithira dothi kumutu.+ 13 Atafika, anapeza Eli atakhala pampando m’mbali mwa msewu, maso ali kunjira, pakuti anali kuchita mantha mumtima mwake chifukwa cha likasa la Mulungu woona.+ Ndiyeno mwamunayo analowa mumzindawo kukanena za nkhondoyo, ndipo anthu onse mumzindawo anayamba kulira. 14 Choncho Eli anamva phokoso la kulira kwa anthuwo, ndipo anati: “Kodi chisokonezo chikuchitika kumeneku n’chachiyani?”+ Kenako mwamuna uja anathamanga kukauza Eli. 15 (Eli anali ndi zaka 98, ndipo maso ake anangokhala tong’o koma sanali kuona.)+ 16 Tsopano mwamuna uja anauza Eli kuti: “Ine ndikuchokera kumalo omenyera nkhondo, ndithudi ndachita kuthawa kumeneko lero.” Pamenepo Eli anam’funsa kuti: “Chachitika n’chiyani mwana wanga?” 17 Choncho munthu wobweretsa uthengayo anayankha kuti: “Aisiraeli athawa pamaso pa Afilisiti, ndipo agonjetsedwa koopsa.+ Ana anunso awiri, Hofeni ndi Pinihasi,+ aphedwa. Ngakhalenso likasa la Mulungu woona lalandidwa.”+

18 Ndiyeno mwamunayo atangotchula za likasa la Mulungu woona, Eli anagwa chagada kuchoka pampando, ali pachipatapo. Chotero khosi lake linathyoka ndipo anafa, pakuti anali wokalamba ndi wonenepa kwambiri. Eli anali ataweruza Isiraeli zaka 40. 19 Mpongozi wake, mkazi wa Pinihasi, anali ndi pakati moti anali pafupi kubereka. Ndiyeno anamva kuti likasa la Mulungu woona lalandidwa ndipo apongozi ake ndi mwamuna wake afa. Zitatero, anawerama n’kuyamba kubereka, chifukwa zowawa za pobereka zinam’fikira mwadzidzidzi.+ 20 Mkaziyu atatsala pang’ono kumwalira, amayi amene anaima pambali pake anayamba kulankhula kuti: “Usachite mantha, pakuti wabereka mwana wamwamuna.”+ Koma iye sanayankhe kapena kuikirapo mtima. 21 Iye anatcha mwanayo kuti Ikabodi,*+ n’kunena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina.”+ Ananena zimenezi chifukwa cha likasa la Mulungu woona limene linali litalandidwa, ndiponso chifukwa cha apongozi ake ndi mwamuna wake.+ 22 Choncho ananena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina,+ chifukwa likasa la Mulungu woona lalandidwa.”+

5 Tsopano Afilisiti anatenga likasa+ la Mulungu woona kuchoka nalo ku Ebenezeri n’kupita nalo ku Asidodi.+ 2 Kumeneko anatenga likasa la Mulungu woona ndi kulilowetsa m’nyumba ya Dagoni, n’kuliika pafupi ndi fano la Dagonilo.+ 3 Tsiku lotsatira Aasidodi anadzuka m’mawa kwambiri, ndipo anapeza Dagoni atagwa pansi chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova.+ Zitatero, anatenga Dagoni ndi kumubwezeretsa pamalo ake.+ 4 Atadzuka m’mawa kwambiri tsiku lotsatira, anapezanso kuti Dagoni wagwa pansi chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Anapeza mutu wa Dagoni ndi zikhatho zake zitaduka ndi kugwera pakhomo.+ Mbali yooneka ngati nsomba* ndi imene inatsala. 5 N’chifukwa chake ansembe a Dagoni ndi anthu onse olowa m’nyumba ya Dagoni ku Asidodi saponda pakhomo la nyumba ya Dagoni mpaka lero.

6 Ndiyeno dzanja la Yehova+ linakhala lamphamvu kwambiri pa Aasidodi, kutanthauza mzinda wa Asidodi ndi madera ake ozungulira, ndipo anayamba kuwasautsa ndi kuwakantha ndi matenda a mudzi.*+ 7 Anthu a ku Asidodi ataona kuti zafika pamenepo, anati: “Musalole kuti likasa la Mulungu wa Isiraeli likhale ndi ife kuno, chifukwa dzanja lake latisautsa kwambiri pamodzi ndi Dagoni mulungu wathu.”+ 8 Chotero anatumiza uthenga ndi kusonkhanitsa olamulira onse ogwirizana a Afilisiti ku Asidodi ndi kuwauza kuti: “Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Isiraeli?” Pamapeto pake iwo anati: “Likasa limeneli la Mulungu wa Isiraeli tilitumize kumzinda wa Gati.”+ Choncho anapititsa likasa la Mulungu wa Isiraeli kumeneko atayenda nalo mozungulira.

9 Kenako zimene zinachitika n’zakuti, atazungulira ndi likasalo n’kufika nalo kumeneko, dzanja la Yehova+ linasautsanso mzindawo ndi chisokonezo chachikulu kwambiri. Iye anayamba kukantha anthu onse a mumzindawo, osasiyapo aliyense moti onsewo anagwidwa ndi matenda a mudzi.+ 10 Choncho anatumiza likasa la Mulungu woona ku Ekironi.+ Ndiyeno likasa la Mulungu woona litangofika ku Ekironi, anthu a ku Ekironi anayamba kulira, kuti: “Atibweretsera likasa la Mulungu wa Isiraeli kuti atiphe ife tonse!”+ 11 Chotero anatumiza uthenga ndi kusonkhanitsa olamulira onse ogwirizana a Afilisiti, n’kuwauza kuti: “Chotsani likasa la Mulungu wa Isiraeli pakati pathu, libwerere kwawo kuti lisatiphe.” Ananena zimenezi chifukwa mumzinda wonsewo+ anthu anali kuopa kuti afa, pakuti dzanja la Mulungu woona linali kuwasautsa kumeneko.+ 12 Anthu amene sanafe anakanthidwa ndi matenda a mudzi.+ Ndipo anthu a mumzindawo anayang’ana kumwamba, kulirira+ thandizo.

6 Likasa+ la Yehova linakhala m’dziko la Afilisiti miyezi 7. 2 Ndiyeno Afilisiti anaitana ansembe ndi alauli,+ ndi kuwafunsa kuti: “Kodi likasa la Yehova tichite nalo chiyani? Tiuzeni zimene tingapereke polibweza kwawo.” 3 Iwo anayankha kuti: “Ngati mukubweza likasa la Mulungu wa Isiraeli, musalibweze osapereka nsembe. Mulimonse mmene zingakhalire, muyenera kupereka nsembe ya kupalamula+ kwa iye. Mukatero mudzachira, ndipo mudzadziwa chifukwa chake sanali kuchotsa dzanja lake pa inu.” 4 Ndiyeno iwo anafunsa kuti: “Kodi nsembe ya kupalamula imene tiyenera kupereka ikhale chiyani?” Poyankha, ansembe ndi alauli aja anati: “Mupereke zifanizo zisanu zagolide za matenda a mudzi, ndi zifanizo zisanu zagolide za mbewa zoyenda modumpha, malinga ndi chiwerengero cha olamulira ogwirizana+ a Afilisiti. Muchite zimenezi pakuti mliri umene wagwera aliyense wa inu, pamodzi ndi olamulira anu ogwirizana ndi umodzi. 5 Ndipo muyenera kupanga zifanizo za matenda anu a mudzi ndi zifanizo za mbewa zoyenda modumpha+ zimene zikuwononga dziko, ndipo mupereke ulemerero+ kwa Mulungu wa Isiraeli. Mukatero, mwina adzachepetsako mphamvu ya dzanja lake pa inu, mulungu wanu ndi dziko lanu.+ 6 Komanso, mukuumitsiranji mitima yanu mmene Aiguputo ndi Farao anaumitsira mitima yawo?+ Si paja Mulungu atangowakhaulitsa+ analola Aisiraeli kupita, ndipo iwo anapitadi?+ 7 Choncho pangani ngolo+ yatsopano, ndipo mutenge ng’ombe ziwiri zoyamwitsa zimene sizinanyamulepo goli+ ndi kuzimangirira kungoloyo. Ana a ng’ombezo muwabweze kunyumba kuti asatsatire amayi awo. 8 Ndiyeno mutenge likasa la Yehova ndi kuliika m’ngoloyo. Zinthu zagolide+ zimene muyenera kupereka monga nsembe ya kupalamula+ muziike m’bokosi lina pambali pa likasa, kenako mulitumize, ndipo lichoke. 9 Ndiyeno muonetsetse izi: Likasalo likadzalowera njira yopita kwawo, ku Beti-semesi,+ ndiye kuti iye ndi amenedi watichitira choipa chachikuluchi. Koma ngati sililowera kumeneko, tidziwa kuti si dzanja lake limene latikhudza, koma ngozi+ yangotigwera.”

10 Chotero anthuwo anachitadi zomwezo. Anatenga ng’ombe ziwiri zoyamwitsa n’kuzimangirira kungoloyo, ndipo ana a ng’ombezo anawatsekera kunyumba. 11 Ndiyeno anaika likasa la Yehova m’ngoloyo.+ Anaikamonso bokosi lina lija lokhala ndi mbewa zoyenda modumpha zagolide ndi zifanizo za matenda awo a mudzi. 12 Ng’ombezo zinayamba kuyenda, kulunjika msewu wa ku Beti-semesi.+ Zinali kuyenda pamsewu waukulu wopita kumeneko zikulira, ndipo sizinapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. Apa n’kuti olamulira ogwirizana+ a Afilisiti akuzitsatira pambuyo mpaka kukafika m’malire a Beti-semesi. 13 Anthu a ku Beti-semesi anali kukolola tirigu+ m’chigwa. Atakweza maso ndi kuona Likasa, anasangalala kwambiri. 14 Ngoloyo inafika m’munda wa Yoswa, amene kwawo kunali ku Beti-semesi, ndi kuima pamalo pamene panali mwala waukulu. Ndiyeno anthuwo anawaza matabwa a ngoloyo ndipo ng’ombezo+ anazipereka nsembe yopsereza kwa Yehova.+

15 Tsopano Alevi+ anatsitsa likasa la Yehova, pamodzi ndi bokosi lina lija mmene munali zinthu zagolide, n’kuliika pamwala waukulu uja. Kenako amuna a ku Beti-semesi+ anapereka nsembe zopsereza, ndipo anapitiriza kupereka nsembe kwa Yehova tsiku limenelo.

16 Olamulira asanu ogwirizana+ a Afilisiti aja anaona zimenezo ndipo anabwerera ku Ekironi tsiku limenelo. 17 Ndiyeno zifanizo zagolide za matenda a mudzi zimene Afilisiti anapereka kwa Yehova monga nsembe ya kupalamula ndi izi:+ mzinda wa Asidodi+ unapereka chifanizo chimodzi, wa Gaza+ chimodzi, wa Asikeloni+ chimodzi, wa Gati+ chimodzi ndi wa Ekironi+ chimodzi. 18 Chiwerengero cha mbewa zoyenda modumpha zagolide chinali chofanana ndi mizinda yonse ya Afilisiti ya olamulira asanu ogwirizana, kuyambira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mpaka ku mudzi wopanda mpanda.

Mwala waukulu umene anakhazikapo likasa la Yehova ndiwo mboni mpaka lero m’munda wa Yoswa, amene kwawo kunali ku Beti-semesi. 19 Chotero Mulungu anakantha anthu a ku Beti-semesi,+ chifukwa anayang’anitsitsa likasa la Yehova. Anakantha anthu 70 [[anthu 50,000]]* pakati pawo, ndipo anthu anayamba kulira chifukwa Yehova anakantha anthuwo koopsa.+ 20 Kenako amuna a ku Beti-semesi ananena kuti: “Ndani angaime pamaso pa Yehova Mulungu woyera,+ ndipo kodi sangatileke n’kupita kwa ena?”+ 21 Pamapeto pake anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-yearimu+ kuti: “Afilisiti abweza likasa la Yehova, bwerani kuno mudzalitenge.”+

7 Chotero amuna a ku Kiriyati-yearimu+ anabweradi ndi kutenga likasa la Yehova n’kupita nalo kwawo, ndipo analiika m’nyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Anapatula Eleazara mwana wake kuti azilondera likasa la Yehova.

2 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, kuchokera pamene Likasa linayamba kukhala ku Kiriyati-yearimu, panapita nthawi yaitali mpaka zinakwana zaka 20. Izi zili choncho, nyumba yonse ya Isiraeli inayamba kulirira Yehova.+ 3 Zitatero, Samueli anauza nyumba yonse ya Isiraeli kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova+ ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu.+ Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti,+ ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina,+ ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”+ 4 Pamenepo ana a Isiraeli anachotsa Abaala+ ndi zifaniziro za Asitoreti+ pakati pawo n’kuyamba kutumikira Yehova yekha.

5 Ndiyeno Samueli anawauza kuti: “Sonkhanitsani Aisiraeli onse+ pamodzi ku Mizipa,+ kuti ndikupempherereni+ kwa Yehova.” 6 Choncho iwo anasonkhana pamodzi ku Mizipa, ndipo anali kutunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova ndi kusala kudya tsiku limenelo.+ Ali kumeneko, anayamba kunena kuti: “Tachimwira Yehova.”+ Pamenepo, Samueli anayamba kuweruza+ ana a Isiraeli ku Mizipa.

7 Tsopano Afilisiti anamva kuti ana a Isiraeli asonkhana pamodzi ku Mizipa. Zitatero olamulira ogwirizana+ a Afilisiti ananyamuka kuti akamenyane ndi Isiraeli. Ana a Isiraeli atamva zimenezi, anachita mantha chifukwa cha Afilisiti.+ 8 Chotero ana a Isiraeli anauza Samueli kuti: “Usakhale chete, koma utipempherere kwa Yehova Mulungu kuti atithandize,+ kuti atipulumutse m’manja mwa Afilisiti.” 9 Ndiyeno Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa ndi kum’pereka nsembe yopsereza, nsembe yathunthu,+ kwa Yehova. Atatero anayamba kupempherera Aisiraeli+ kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anamuyankha.+ 10 Pamene Samueli anali kupereka nsembe yopsereza, Afilisiti anayandikira kuti amenyane ndi Isiraeli. Zitatero, Yehova anachititsa mabingu amphamvu kwambiri+ pa tsiku limenelo kuti asokoneze Afilisiti.+ Choncho Afilisitiwo anagonjetsedwa pamaso pa Isiraeli.+ 11 Pamenepo amuna a Isiraeli anatuluka kuchokera ku Mizipa ndi kuthamangitsa Afilisiti, ndipo anawakantha mpaka kum’mwera kwa Beti-kara. 12 Kenako Samueli anatenga mwala+ ndi kuuimika pakati pa Mizipa ndi Yesana ndipo anautcha dzina lakuti Ebenezeri,* n’kunena kuti: “Lero Yehova watithandiza ngati kale.”+ 13 Chotero Afilisiti anagonjetsedwa ndipo sanabwerenso m’dziko la Isiraeli.+ Dzanja la Yehova linapitiriza kukankhira kutali Afilisiti masiku onse a moyo wa Samueli.+ 14 Pamenepo, mizinda imene Afilisitiwo analanda Isiraeli inayamba kubwerera kwa Isiraeli, kuyambira ku Ekironi mpaka ku Gati, ndipo Aisiraeli analanda dera la mizindayo m’manja mwa Afilisiti.

Choncho panakhala mtendere pakati pa Isiraeli ndi Aamori.+

15 Samueli anapitiriza kuweruza Isiraeli masiku onse a moyo wake.+ 16 Chaka ndi chaka Samueli anali kuzungulira m’madera a Beteli,+ Giligala+ ndi Mizipa,+ ndipo anali kuweruza+ Isiraeli m’malo onsewa. 17 Akazungulirazungulira, anali kubwerera ku Rama,+ chifukwa kumeneko n’kumene kunali nyumba yake, ndipo anali kuweruza Isiraeli ali kumeneko. Komanso iye anamangira Yehova guwa lansembe kumeneko.+

8 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Samueli atakalamba anaika+ ana ake aamuna kukhala oweruza mu Isiraeli. 2 Mwana wake woyamba dzina lake anali Yoweli,+ ndipo mwana wake wachiwiri anali Abiya.+ Amenewa anali oweruza ku Beere-seba. 3 Ana akewa sanatsatire chitsanzo chake,+ koma anali okonda kupeza phindu mwachinyengo,+ ndipo anali kulandira ziphuphu+ ndi kupotoza chiweruzo.+

4 Patapita nthawi, akulu onse a mu Isiraeli+ anasonkhana pamodzi n’kupita kwa Samueli ku Rama. 5 Atafika kumeneko anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba, koma ana ako sakutsatira chitsanzo chako. Ndiye tikufuna kuti utiikire mfumu+ yoti izitiweruza ngati mitundu ina yonse.” 6 Koma zimenezi zinamuipira Samueli, chifukwa iwo anati: “Utipatse mfumu yoti izitiweruza.” Pamenepo Samueli anayamba kupemphera kwa Yehova.+ 7 Poyankha, Yehova anauza Samueli+ kuti: “Mvera zonse zimene anthuwo akunena kwa iwe,+ pakuti sanakane iweyo koma akana ine kuti ndisakhale mfumu yawo.+ 8 Zinthu zonse zimene akhala akuchita kuyambira pa tsiku limene ndinawatulutsa mu Iguputo+ mpaka lero, kundisiya+ n’kumakatumikira milungu ina,+ n’zimenenso akuchitira iwe. 9 Choncho mvera mawu awo. Koma uwachenjeze mwamphamvu, ndipo uwauze zimene mfumu imene iziwalamulirayo izidzafuna kwa iwo.”+

10 Samueli anafotokozera anthu amene anali kum’pempha kuti awaikire mfumuwo mawu onse a Yehova. 11 Iye anawauza kuti: “Izi ndi zimene mfumu yokulamuliraniyo izidzafuna kwa inu:+ Idzatenga ana anu+ kuti azikayenda m’magaleta*+ ake ndi kukwera pamahatchi*+ ake, ndipo ena mwa ana anuwo azidzathamanga patsogolo pa magaleta ake.+ 12 Idzaika anthu ena kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 50.+ Ena azidzalima minda yake+ ndi kukolola mbewu zake,+ ndiponso ena azidzapanga zida zake zankhondo+ ndi zida zogwiritsa ntchito pamagaleta ake.+ 13 Ana anu aakazi idzawatenga kuti akakhale opanga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi opanga mkate.+ 14 Mfumuyo idzakulandani minda yanu yabwino kwambiri, minda ya mbewu, ya mpesa+ ndi ya maolivi+ n’kupatsa antchito ake. 15 Idzatenganso gawo limodzi mwa magawo 10+ a zokolola za m’minda yanu ya mbewu ndi ya mpesa, n’kuzipereka kwa nduna za panyumba ya mfumu+ ndi kwa antchito ake. 16 Antchito anu aamuna, antchito anu aakazi, abusa anu aluso kwambiri ndi abulu anu idzawatenganso kuti ikawagwiritse ntchito.+ 17 Pa zoweta zanu+ idzatengapo gawo limodzi mwa magawo 10, ndipo inuyo mudzakhala antchito ake. 18 Ndipo mudzalira pa tsiku limenelo chifukwa cha mfumu yanu+ imene mwadzisankhira nokha, koma Yehova sadzakuyankhani.”+

19 Koma anthuwo anakana kumvera mawu a Samueli+ ndipo anati: “Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulira. 20 Ifenso tikufuna kukhala ngati mitundu ina yonse,+ ndipo mfumu yathuyo ndi imene izitiweruza ndi kutitsogolera kukamenya nkhondo zathu.” 21 Samueli anamvera mawu onse amene anthuwo ananena, kenako anafotokozera Yehova mawuwo.+ 22 Zitatero Yehova anauza Samueli kuti: “Mvera mawu awo ndipo uwaikire mfumu yoti iziwalamulira.”+ Chotero Samueli anauza amuna a Isiraeli kuti: “Aliyense wa inu apite kumzinda wakwawo.”

9 Tsopano panali mwamuna wina wochokera kudera la Benjamini dzina lake Kisi,+ mwana wa Abiyeli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. Iye anali wa fuko la Benjamini+ ndipo anali mwamuna wachuma kwambiri.+ 2 Iyeyu anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Sauli,+ mnyamata wokongola, ndipo panalibe munthu wina mwa ana a Isiraeli wokongola ngati iyeyu. Sauli anali wam’tali kwambiri moti panalibe munthu aliyense amene anali kum’pitirira m’mapewa ake.+

3 Ndiyeno abulu aakazi+ a Kisi bambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anauza Sauli mwana wake kuti: “Tenga mmodzi mwa atumikiwa ndipo upite kukafunafuna abulu aakazi.” 4 Ndiyeno anayenda kudutsa m’dera lamapiri la Efuraimu+ mpaka kukadutsanso m’dera la Salisa,+ koma abuluwo sanawapeze. Atatero anadutsa m’dera la Saalimu, ndipo sanawapezenso kumeneko. Kenako anadutsa m’dera la Abenjamini, koma kumenekonso sanawapeze.

5 Ndiyeno iwo anafika m’dera la Zufi. Pamenepo Sauli anauza mtumiki wake kuti: “Tiye tibwerere kunyumba, chifukwa bambo anga angasiye kuganizira za abulu aakazi n’kuyamba kuda nkhawa za ife.”+ 6 Koma mtumikiyo anamuyankha kuti: “Mumzinda uwu mulitu munthu wa Mulungu,+ ndipo ndi munthu wolemekezeka. Zonse zimene wanena sizilephera, zimachitikadi.+ Ndiye tiye tipite kumeneko, mwina angatiuze kumene tingalowere.” 7 Koma Sauli anafunsa mtumiki wakeyo kuti: “Ndiye tikapita kumeneko tikam’patsa chiyani?+ Tilibe mphatso+ imene tingapatse munthu wa Mulungu woonayo, chifukwanso mkate watha m’zotengera zathu. Tili ndi chiyani?” 8 Poyankha mtumikiyo anauzanso Sauli kuti: “Inetu ndili ndi gawo limodzi mwa magawo anayi a sekeli*+ la siliva loti ndingam’patse munthu wa Mulungu woonayo ndipo adzatiuza kumene tingalowere.” 9 (Kalekale mu Isiraeli, munthu akafuna kukafunsira kwa Mulungu ankanena kuti: “Tiyeni tipite kwa wamasomphenya.”*+ Pakuti amene amatchedwa mneneri masiku ano, kalekalelo anali kutchedwa kuti wamasomphenya.) 10 Pamenepo Sauli anauza mtumiki wakeyo kuti: “Wanena bwino.+ Tiye tizipita.” Ndipo analowera kumzindawo, kumene kunali munthu wa Mulungu woona.

11 Pokwezeka chitunda kuti akalowe mumzindawo, iwo anakumana ndi atsikana akupita kukatunga madzi,+ ndipo anawafunsa kuti: “Kodi wamasomphenya+ alipo mumzindawu?” 12 Iwo anawayankha kuti: “Ee, alipo. Mum’peza kumene mukupitaku. Fulumirani, wafika lero mumzinda chifukwa lero anthu apereka nsembe+ pamalo okwezeka.+ 13 Mukangolowa mumzinda, mum’peza ndithu asanapite kukadya kumalo okwezeka. Anthu sangayambe kudya pokhapokha iye atafika, chifukwa ndiye amadalitsa nsembeyo.+ Kenako oitanidwa amadya. Choncho pitani chifukwa mum’peza posachedwapa.” 14 Chotero, anapita kukalowa mumzindawo. Pamene anali kuyandikira pakati pa mzinda, anangoona Samueli watulukira kudzakumana nawo kuti apite kumalo okwezeka.

15 Koma dzulo lake, Sauli asanafike, Yehova anali atauziratu+ Samueli kuti: 16 “Mawa nthawi ngati ino ndikutumizira munthu kuchokera kudera la Benjamini,+ ndipo udzam’dzoze+ kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli. Iye adzapulumutsa anthu anga m’manja mwa Afilisiti,+ chifukwa ndaona kusautsika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”+ 17 Samueli ataona Sauli, Yehova anamuuza kuti: “Ameneyu ndiye munthu ndimakuuza uja kuti, ‘Ameneyo ndiye adzalamulire anthu anga.’”+

18 Pamenepo Sauli analunjika Samueli pakati pa mzinda ndi kunena kuti: “Ndifunseko, Kodi nyumba ya wamasomphenya ili kuti?” 19 Ndipo Samueli anayankha Sauli kuti: “Wamasomphenyayo ndineyo. Tsogola tipite kumalo okwezeka ndipo inuyo mudya ndi ine lero.+ Ndidzakulolani kupita mawa m’mawa, ndipo ndikuuzani zonse zimene mukufuna kudziwa.+ 20 Koma za abulu aakazi amene anasowa masiku atatu apitawo+ musadandaule,+ chifukwa anapezeka. Kodi zabwino zonse mu Isiraeli ndi za ndani?+ Kodi si zako ndi nyumba yonse ya bambo ako?” 21 Pamenepo Sauli anayankha kuti: “Kodi ine si wa m’fuko la Benjamini, fuko laling’ono kwambiri+ pa mafuko onse a Isiraeli?+ Ndipo kodi banja langa sindilo laling’ono kwambiri pa mabanja onse a m’fuko la Benjamini?+ Ndiye n’chifukwa chiyani mwalankhula mawu otere kwa ine?”+

22 Ndiyeno Samueli anatenga Sauli pamodzi ndi mtumiki wake n’kupita nawo m’chipinda chodyera. Mmenemo anawapatsa malo apamwamba kwambiri+ pakati pa oitanidwa. M’chipindamo munali anthu 30. 23 Kenako Samueli anauza wophika kuti: “Ndipatse nyama ndinakupatsa ija, imene ndinakuuza kuti uisunge.” 24 Pamenepo wophikayo anatenga mwendo wonse n’kuuika patsogolo pa Sauli. Atatero anati: “Nyama imene inasungidwa ija ndi imeneyi. Tenga, udye chifukwa anasungira iweyo kuti udzaidye pa nthawi ino pamodzi ndi oitanidwa.” Chotero Sauli anadya pamodzi ndi Samueli pa tsikulo. 25 Zitatero, anatsika kumalo okwezeka+ aja n’kukalowa mumzinda, ndipo Samueli anapitiriza kulankhula ndi Sauli ali padenga* la nyumba.+ 26 Ndiyeno Samueli ndi Sauli anadzuka m’mawa kwambiri, m’bandakucha, ndipo Samueli, ali padenga la nyumba, anaitana Sauli ndi kumuuza kuti: “Konzekera ulendo.” Pamenepo Sauli ananyamuka ndipo onse awiri, iyeyo ndi Samueli, anatuluka kupita panja. 27 Pamene anali kupita kumalire a mzindawo, Samueli anauza Sauli kuti: “Uza mtumiki wako+ kuti atsogole, koma iwe ima kaye kuti ndikuuze mawu a Mulungu.” Atatero, mtumikiyo anatsogola.

10 Ndiyeno Samueli anatenga+ botolo ladothi la mafuta ndi kutsanulira mafutawo pamutu wa Sauli, n’kumupsompsona+ ndi kunena kuti: “Yehova wakudzoza iwe kukhala mtsogoleri+ wa cholowa chake.+ 2 Lero ukasiyana ndi ine, ukumana ndi amuna awiri pafupi ndi manda a Rakele+ pa Zeliza, m’dera la Benjamini. Iwo akuuza kuti, ‘Abulu aakazi+ amene unapita kukafunafuna anapezeka, moti bambo ako sakuganiziranso za abulu aakaziwo koma ayamba kudera nkhawa za inuyo, moti akunena kuti: “Nditani ine pakuti mwana wanga sakuoneka?”’+ 3 Kuchoka pamenepo upitirize ulendo wako mpaka kukafika kumtengo waukulu wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi amuna atatu akupita ku Beteli+ kukapembedza Mulungu woona. Mmodzi wa iwo akhala atanyamula ana atatu a mbuzi,+ wina atanyamula mitanda yobulungira itatu ya mkate,+ ndipo winayo atanyamula mtsuko waukulu wa vinyo.+ 4 Amunawo akulonjera+ ndi kukupatsa mitanda iwiri ya mkate, ndipo uilandire. 5 Ukachoka pamenepo ufika kuphiri la Mulungu woona,+ kumene kuli mudzi wa asilikali+ a Afilisiti. Ndiyeno zimene zichitike n’zakuti, poyandikira mzindawo, ukumana ndi kagulu ka aneneri+ akuchokera kumalo okwezeka,+ akulankhula monga aneneri. Patsogolo pawo pakhala pali choimbira cha zingwe,+ maseche,+ chitoliro+ ndi zeze.+ 6 Pamenepo mzimu+ wa Yehova uyamba kugwira ntchito pa iwe, moti iweyo uyamba kulankhula monga mneneri+ pamodzi ndi aneneriwo, ndiponso usinthika kukhala wina. 7 Ndiyeno zizindikiro+ zimenezi zikachitika pa iwe, uchite chilichonse chimene ungathe,+ chifukwa Mulungu woona ali ndi iwe.+ 8 Choncho utsogole kupita ku Giligala.+ Inenso ndipita kumeneko kuti ndikapereke nsembe zopsereza ndi kupereka nsembe zachiyanjano.+ Ukandidikire masiku 7+ mpaka nditakupeza, ndipo ndikadzafika ndidzakuuza zoti uchite.”

9 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Sauli atangotembenuka kuti asiyane ndi Samueli, Mulungu anayamba kusintha mtima wake kukhala wina,+ moti zizindikiro+ zonsezi zinayamba kuchitikadi pa tsiku limenelo. 10 Chotero Sauli ndi mtumiki wake ananyamuka kupita kuphiri kuja, ndipo kumeneko anakumana ndi kagulu ka aneneri. Nthawi yomweyo, mzimu wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye,+ moti anayamba kulankhula ngati mneneri+ pakati pa aneneriwo. 11 Ndiyeno onse amene anali kumudziwa atamuona, anadabwa kuona kuti ali pakati pa aneneri ndipo akulankhula ngati mneneri. Choncho anthuwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi chachitikira mwana wa Kisi n’chiyani? Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+ 12 Mmodzi wa iwo poyankha anati: “Koma kodi bambo wawo ndani?” N’chifukwa chake pali mawu okuluwika+ akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”

13 Patapita nthawi anamaliza kulankhula ngati mneneri, ndipo anafika kumalo okwezeka. 14 Kenako m’bale wa bambo ake a Sauli anafunsa Sauli pamodzi ndi mtumiki wake kuti: “Kodi munapita kuti?” Poyankha iye anati: “Tinapita kukafunafuna abulu aakazi,+ moti tinali kungoyendabe kuwafufuza, koma sitinawapeze. Choncho tinapita kwa Samueli.” 15 Pamenepo m’bale wa bambo ake a Sauli anati: “Ndiuzeni chonde, Kodi Samueli anakuuzani chiyani?” 16 Sauli anayankha m’bale wa bambo akeyo kuti: “Anatiuza mosaphonyetsa kuti abulu aakazi anali atapezeka.” Koma iye sananene za nkhani ya ufumu imene Samueli anamuuza.+

17 Tsopano Samueli anasonkhanitsa anthu onse pamodzi pamaso pa Yehova ku Mizipa+ 18 ndi kuuza ana a Isiraeliwo kuti: “Mverani zimene Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena,+ ‘Ndine amene ndinatulutsa Isiraeli mu Iguputo,+ amenenso ndinakupulumutsani m’manja mwa Aiguputo ndi m’manja mwa maufumu onse amene anali kukuponderezani.+ 19 Koma inu, lero mwakana Mulungu wanu+ amene anakupulumutsani m’masautso anu onse ndi m’zowawa zanu, kufika ponena kuti: “Ife tikufuna kuti utiikire mfumu yoti izitilamulira.” Tsopano imani pamaso pa Yehova malinga ndi mafuko anu+ ndi mabanja anu.’”*

20 Chotero Samueli anabweretsa mafuko onse a Isiraeli pafupi,+ ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa.+ 21 Kenako anabweretsa pafupi fuko la Benjamini malinga ndi mabanja awo, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa.+ Pamapeto pake, Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa.+ Choncho anayamba kum’funafuna, koma sanam’peze. 22 Motero anafunsiranso+ kwa Yehova, kuti: “Kodi mwamunayu wafika kale pano?” Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Uyu wabisala+ pakati pa katunduyu.” 23 Choncho anthu anathamanga kukam’tenga kumeneko. Ataimirira pakati pa anthuwo, anali wam’tali kwambiri moti panalibe munthu aliyense amene anali kum’pitirira m’mapewa ake.+ 24 Ndiyeno Samueli anauza anthu onsewo kuti: “Kodi mwaona amene Yehova wam’sankha,+ kuti palibe aliyense pakati pa anthu onse wofanana naye?” Pamenepo anthu onsewo anayamba kufuula, kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+

25 Zitatero, Samueli anauza anthuwo zinthu zimene mfumu iyenera kulandira kwa iwo+ ndipo anazilemba m’buku limene analiika pamaso pa Yehova. Kenako Samueli anauza anthuwo kuti aliyense abwerere kwawo. 26 Koma Sauli anapita kwawo ku Gibeya,+ ndipo amuna olimba mtima amene Mulungu anakhudza mitima yawo anapita naye pamodzi.+ 27 Koma anthu opanda pake+ anali kunena kuti: “Kodi ameneyu angatipulumutse bwanji?”+ Chotero anamunyoza,+ moti sanam’bweretsere mphatso iliyonse.+ Koma Sauli anangokhala chete.+

11 Ndiyeno Nahasi Muamoni+ anapita kukamanga msasa kuti amenyane ndi mzinda wa Yabesi+ ku Giliyadi. Zitatero, amuna onse a ku Yabesi anauza Nahasi kuti: “Chita nafe pangano kuti tizikutumikira.”+ 2 Kenako Nahasi Muamoni ananena kuti: “Ndidzachita nanu pangano pokhapokha nditaboola diso+ la kudzanja lamanja la aliyense wa inu, kuti chikhale chinthu chotonzetsa Aisiraeli onse.”+ 3 Poyankha akulu a ku Yabesi anati: “Utipatse masiku 7 kuti titumize amithenga m’dziko lonse la Isiraeli, ndipo ngati sipapezeka wotipulumutsa,+ pamenepo tibwera kwa iwe.” 4 Mithengayo inafika ku Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, ndi kuuza anthu uthengawo. Anthu onse atamva uthengawo anayamba kulira mokweza mawu.+

5 Ndiyeno Sauli anatulukira kuchokera kutchire, akuyenda pambuyo pa ziweto. Kenako anati: “Kodi chachitika n’chiyani kuti anthuwa azilira?” Motero anayamba kum’fotokozera mawu a amuna a ku Yabesi. 6 Sauli atamva mawu amenewa mzimu+ wa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo anapsa mtima kwambiri.+ 7 Iye anatenga ng’ombe ziwiri zamphongo n’kuziduladula. Kenako anatumiza amithenga kukapereka zigawo za ng’ombezo m’dziko lonse la Isiraeli+ ndipo anati: “Aliyense amene satsatira Sauli ndi Samueli, izi n’zimene zichitikire ng’ombe zake.”+ Anthu atamva mawu amenewa anagwidwa ndi mantha+ ochokera kwa Yehova,+ moti onse anapita mogwirizana.+ 8 Ndiye anatenga onsewo+ ndi kupita nawo ku Bezeki. Ana a Isiraeli analipo 300,000, ndipo amuna a ku Yuda analipo 30,000. 9 Tsopano iwo anauza amithenga amene anabwerawo kuti: “Anthu a ku Yabesi ku Giliyadi mukawauze kuti, ‘Mawa mulandira chipulumutso dzuwa litatentha.’”+ Pamenepo amithenga aja anafika ku Yabesi ndi kuuza anthu a kumeneko uthengawo moti anthuwo anasangalala kwambiri. 10 Choncho anthu a ku Yabesi anati: “Mawa tifika kwa inu, ndipo mutichitire chilichonse chimene chingakukomereni m’maso mwanu.”+

11 Tsiku lotsatira, Sauli+ anagawa anthuwo m’magulu atatu.+ Amenewa analowa pakati pa msasawo pa ulonda wa m’mawa.*+ Atatero, anayamba kukantha Aamoni+ kufikira dzuwa litatentha. Otsala anawabalalitsa moti sipanatsale anthu awiri ali limodzi.+ 12 Tsopano anthuwo anayamba kuuza Samueli kuti: “Ndani akunena kuti, ‘Sauli sangakhale mfumu yathu?’+ Tipatseni anthu amenewo tiwaphe.”+ 13 Koma Sauli anayankha kuti: “Lero pasaphedwe munthu aliyense,+ chifukwa Yehova watipulumutsa mu Isiraeli.”+

14 Kenako Samueli anauza anthuwo kuti: “Tiyeni tipite ku Giligala+ kuti tikachitenso mwambo wolonga mfumu.”+ 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo analonga Sauli kukhala mfumu pamaso pa Yehova ku Giligalako. Kenako anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova+ kumeneko, ndipo Sauli pamodzi ndi amuna onse a Isiraeli anali osangalala kwambiri.+

12 Pamapeto pake Samueli anauza Aisiraeli onse kuti: “Ndamva mawu anu onse amene munandiuza,+ kuti ndikuikireni mfumu yokulamulirani.+ 2 Tsopano si iyi mfumu ikuyenda patsogolo panu!+ Koma ine, ndakalamba+ ndipo ndachita imvi.+ Ana anga aamuna, si awa ali pakati panu,+ ndipo ine ndatumikira Mulungu ndi kukutsogolerani kuyambira pa ubwana wanga, mpaka lero.+ 3 Ine ndaima pamaso panu. Munditsutse pamaso pa Yehova ndi pamaso pa wodzozedwa+ wake: Alipo kodi amene ndinam’tengerapo ng’ombe kapena bulu wake?+ Alipo kodi amene ndinam’chitirapo chinyengo, kapena kum’pondereza? Kodi ndinalandirapo chiphuphu kwa aliyense kuti ndisaone zimene anachita?+ Ndili wokonzeka kukubwezerani anthu inu.”+ 4 Poyankha iwo anati: “Sunatichitire chinyengo, kutipondereza, kapena kulandira chilichonse kwa aliyense wa ife.”+ 5 Atatero, iye anawayankha kuti: “Yehova ndi mboni yokutsutsani, ndipo wodzozedwa+ wake ndi mboni lero kuti simunandipeze ndi mlandu uliwonse.”+ Pamenepo iwo anati: “Inde, iyedi ndi mboni.”

6 Ndiyeno Samueli anauza anthuwo kuti: “Yehova ndiye mboni, iye amene anagwiritsa ntchito Mose ndi Aroni, amenenso anatulutsa makolo anu m’dziko la Iguputo.+ 7 Tsopano imani pomwepa, kuti ndikuweruzeni pamaso pa Yehova ndi kukusimbirani ntchito zonse zolungama+ za Yehova, zimene wachitira inuyo ndi makolo anu.

8 “Yakobo atangofika mu Iguputo,+ makolo anu n’kuyamba kupempha thandizo+ kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose+ ndi Aroni kuti atsogolere makolo anu potuluka mu Iguputo, ndipo anawapatsa dziko lino kuti akhalemo.+ 9 Atatero iwo anaiwala Yehova Mulungu wawo,+ moti anawagulitsa+ kwa Sisera+ mkulu wa gulu lankhondo la Hazori, komanso kwa Afilisiti+ ndi kwa mfumu ya Mowabu,+ ndipo onsewa anapitiriza kumenyana nawo. 10 Choncho anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize,+ ndipo anati, ‘Tachimwa,+ pakuti tasiya Yehova kuti titumikire Abaala+ ndi zifaniziro za Asitoreti.+ Tsopano tilanditseni+ m’manja mwa adani athu, kuti tikutumikireni.’ 11 Pamenepo Yehova anatumiza Yerubaala,+ Bedani, Yefita+ ndi Samueli+ ndipo anakulanditsani m’manja mwa adani anu onse okuzungulirani, kuti mukhale popanda chokuopsani.+ 12 Mutaona kuti mfumu ya ana a Amoni, Nahasi,+ yabwera kudzamenyana nanu, munayamba kundiuza kuti, ‘Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulira!’+ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mfumu yanu.+ 13 Tsopano mfumu imene mwasankha ndi imeneyi, mfumu imene mwapempha.+ Ndipotu Yehova wakuikiranidi mfumu+ yoti izikulamulirani. 14 Ngati mudzaopa Yehova,+ n’kumutumikiradi+ ndi kumvera mawu ake,+ ndipo ngati simudzapandukira+ malamulo a Yehova, Yehova Mulungu wanu adzakhala nanu, inuyo pamodzi ndi mfumu yokulamuliraniyo. 15 Koma ngati simudzamvera mawu a Yehova,+ moti n’kupandukiradi malamulo a Yehova,+ dzanja la Yehova lidzatsutsana ndi inu ndi abambo anu.+ 16 Tsopano, imani pomwepa kuti muonenso chinthu chachikuluchi chimene Yehova achite pamaso panu. 17 Kodi ino si nyengo yokolola tirigu?+ Ndifuulira+ Yehova kuti abweretse mabingu ndi mvula.+ Pamenepo mudziwa ndi kuona kuti choipa chimene mwachita pamaso pa Yehova n’chachikulu,+ pakuti mwapempha kuti mukhale ndi mfumu.”

18 Choncho Samueli anafuulira Yehova,+ moti Yehova anadzetsa mabingu ndi mvula tsiku limenelo.+ Pamenepo anthu onse anachita mantha kwambiri ndi Yehova ndiponso ndi Samueli. 19 Zitatero, anthu onse anayamba kuuza Samueli kuti: “Pempherera+ atumiki ako kwa Yehova Mulungu wako, chifukwa sitikufuna kufa. Pakuti tawonjeza choipa china pa machimo athu onse, mwa kupempha kuti tikhale ndi mfumu.”

20 Pamenepo Samueli anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Inuyo mwachita choipa chachikulu chimenechi. Ngakhale kuti zili choncho, musapatuke n’kusiya kutsatira Yehova,+ koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse.+ 21 Musapatuke kuti mutsatire milungu yopanda pake,+ yopanda phindu,+ imene singakulanditseni, pakuti ndi yopanda pake. 22 Chifukwa cha dzina lake lalikulu,+ Yehova sadzasiya+ anthu ake, pakuti Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.+ 23 Komanso, n’zosatheka kuti ineyo ndichimwire Yehova mwa kusiya kukupemphererani.+ Ndipo ndiyenera kukulangizani+ za njira yabwino+ ndi yolondola. 24 Koma muziopa+ Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse m’choonadi.+ Kumbukirani zinthu zazikulu zimene Yehova wakuchitirani.+ 25 Koma mukachita zinthu zoipa mouma khosi, mudzasesedwa,+ inu pamodzi ndi mfumu yanuyo.”+

13 Sauli anali ndi zaka [?]* pamene anayamba kulamulira,+ ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 2 Ndiyeno Sauli anadzisankhira amuna 3,000 a mu Isiraeli. Amuna 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi+ ndi kudera lamapiri la Beteli. Amuna 1,000 anali ndi Yonatani+ ku Gibeya+ wa ku Benjamini, ndipo anthu ena onse otsalawo anawabweza kumahema awo. 3 Kenako Yonatani anakantha mudzi wa asilikali+ a Afilisiti+ umene unali ku Geba,+ ndipo Afilisiti anamva zimenezi. Zitatero Sauli analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ m’dziko lonse n’kunena kuti: “Imvani Aheberi inu!” 4 Isiraeli yense anamva anthu akukamba kuti: “Sauli wakantha mudzi wa asilikali a Afilisiti, ndipo tsopano Isiraeli wakhala chinthu chonunkha+ kwa Afilisiti.” Choncho anasonkhanitsa anthu onse pamodzi kuti atsatire Sauli ku Giligala.+

5 Afilisiti nawonso anasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi Isiraeli. Iwo anali ndi magaleta ankhondo 30,000,*+ asilikali okwera pamahatchi 6,000 ndi anthu ochuluka kwambiri ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Chotero anapita ku Mikimasi ndi kumanga misasa kum’mawa kwa Beti-aveni.+ 6 Ndipo amuna a Isiraeli anaona kuti zinthu zawathina,+ chifukwa anthu onse anali atapanikizika. Anthuwo anapita kukabisala m’mapanga,+ m’maenje, kumatanthwe, m’zipinda za pansi ndi m’zitsime zopanda madzi. 7 Aheberi ena mpaka anawoloka Yorodano+ kupita m’dera la Gadi+ ndi la Giliyadi. Koma Sauli anali adakali ku Giligala, ndipo anthu onse anali kunjenjemera pamene anali kum’tsatira.+ 8 Sauli anapitiriza kudikira kwa masiku 7 kufikira nthawi yoikidwiratu imene Samueli ananena.+ Koma Samueli sanafikebe ku Giligala, moti anthu anayamba kubalalika kum’siya Sauli. 9 Kenako Sauli anati: “Bweretsani kuno nsembe yopsereza ndi nsembe zachiyanjano.” Pamenepo iye anapereka nsembe yopserezayo.+

10 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo anaona Samueli akubwera. Choncho Sauli anatuluka kukakumana naye ndi kumulonjera.+ 11 Kenako Samueli anati: “N’chiyani chimene wachita?”+ Poyankha Sauli anati: “Nditaona kuti anthu akubalalika kundisiya ndekha,+ ndipo inu simunabwere m’masiku amene munanena aja,+ komanso kuti Afilisiti anali kusonkhana pamodzi ku Mikimasi,+ 12 ndinaganiza+ kuti, ‘Tsopano Afilisitiwa abwera ku Giligala kuno kudzamenyana nane, ndipo sindinakhazike pansi mtima wa Yehova kuti atikomere mtima.’ Choncho ndakakamizika+ kupereka nsembe yopsereza.”

13 Pamenepo Samueli anauza Sauli kuti: “Wachita chinthu chopusa.+ Sunatsatire lamulo+ limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.+ Ukanatsatira lamulo limeneli, Yehova akanalimbitsa ufumu wako pa Isiraeli mpaka kalekale. 14 Tsopano ufumu wako sukhalitsa.+ Yehova apeza munthu wapamtima pake,+ ndipo Yehova amuika kukhala mtsogoleri+ wa anthu ake chifukwa iwe sunasunge zimene Yehova anakulamula.”+

15 Kenako Samueli ananyamuka kuchoka ku Giligala kupita ku Gibeya wa ku Benjamini. Ndiyeno Sauli anayamba kuwerenga anthu amene anali nayebe limodzi, ndipo anapeza amuna pafupifupi 600.+ 16 Choncho Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi anthu amene anali nawo aja, anali kukhala ku Geba+ wa ku Benjamini. Koma Afilisiti anali atamanga msasa ku Mikimasi.+ 17 Anthu olanda katundu anali kutuluka mumsasa wa Afilisiti m’magulu atatu.+ Gulu loyamba linali kulowera kumsewu wopita ku Ofira,+ kudera la Suwali. 18 Gulu lachiwiri linali kulowera kumsewu wa ku Beti-horoni,+ ndipo gulu lachitatu linali kulowera kumsewu wopita kumalire oyang’anana ndi chigwa cha Zeboyimu, molunjika kuchipululu.

19 Ndipo m’dziko lonse la Isiraeli munalibe wosula zitsulo. Izi zinali choncho chifukwa Afilisiti anati: “Aheberi asasule lupanga kapena mkondo.”+ 20 Choncho Aisiraeli onse akafuna kunola pulawo, khasu, nkhwangwa kapena chikwakwa, aliyense wa iwo anali kupita kwa Afilisiti kuti amunolere.+ 21 Ndipo malipiro onoletsera mapulawo, makasu, mafoloko a mano atatu ndi nkhwangwa, ndiponso kukonza chisonga chotosera ng’ombe anali pimu* imodzi.+ 22 Ndiye zinali kuchitika kuti, pa tsiku lankhondo panalibe munthu aliyense mwa anthu amene anali ndi Sauli ndi Yonatani, amene anali ndi lupanga+ kapena mkondo m’manja mwake. Koma Sauli+ yekha ndi mwana wake Yonatani ndi amene anali ndi zida.

23 Tsopano gulu la asilikali+ a Afilisiti linali kutuluka mumsasa ndi kupita kumalo owolokera a ku Mikimasi.+

14 Ndiyeno tsiku lina zinachitika kuti Yonatani+ mwana wa Sauli anauza mtumiki wake womunyamulira zida kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa asilikali a Afilisiti umene uli patsidyapo.” Koma Yonatani sanauze bambo ake zimenezi.+ 2 Pa nthawiyi Sauli anali kukhala kunja kwa mzinda wa Gibeya+ pansi pa mtengo wa makangaza* umene uli ku Migironi. Iye anali ndi amuna pafupifupi 600.+ 3 (Ahiya ndiye anali kunyamula efodi.+ Iye anali mwana wa Ahitubu,+ m’bale wa Ikabodi,+ mwana wa Pinihasi,+ mwana wa Eli,+ wansembe wa Yehova ku Silo.)+ Koma anthu sanadziwe kuti Yonatani wachoka. 4 Tsopano pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kudutsa kuti akamenyane ndi mudzi wa asilikali+ a Afilisiti, panali thanthwe looneka ngati dzino kumbali ina, ndi lina looneka ngati dzino kumbali inanso. Limodzi mwa matanthwewo dzina lake linali Bozezi ndipo linalo linali Sene. 5 Thanthwe limodzi looneka ngati dzinolo linali kumpoto ndipo linaima ngati chipilala moyang’ana ku Mikimasi,+ ndipo linalo linali kum’mwera moyang’ana ku Geba.+

6 Choncho Yonatani anauza mtumiki wake womunyamulira zida uja kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa amuna osadulidwawa.+ Pakuti mwina Yehova adzatithandiza, chifukwa palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.”+ 7 Pamenepo mtumiki wakeyo anamuuza kuti: “Chita zimene mtima wako ukufuna. Tiye kulikonse kumene ukufuna. Ine ndili nawe limodzi kuti ndichite zofuna za mtima wako.”+ 8 Ndiyeno Yonatani anati: “Tsopano tikuwoloka kupita kwa anthuwa, ndipo tidzionetsere kwa iwo. 9 Iwo akatiuza kuti, ‘Imani pomwepo, ife tikubwera kumeneko!’ ife tiimedi pomwepo, osapitiriza kupita kumene iwo ali. 10 Koma akatiuza kuti, ‘Bwerani kuno mudzamenyane nafe!’ ife tipita chifukwa Yehova adzawaperekadi m’manja mwathu, ndipo chimenechi ndicho chizindikiro chathu.”+

11 Atatero, onse awiri anadzionetsera kumudzi wa asilikali a Afilisiti, ndipo Afilisitiwo anayamba kunena kuti: “Taonani Aheberi akutuluka m’maenje amene anabisala.”+ 12 Pamenepo amuna a m’mudzi wa asilikaliwo anauza Yonatani ndi mtumiki wake uja kuti: “Bwerani kuno, ndipo tikukhaulitsani!”+ Nthawi yomweyo Yonatani anauza mtumiki wakeyo kuti: “Nditsatire chifukwa Yehova awapereka ndithu amenewa m’manja mwa Isiraeli.”+ 13 Ndiyeno Yonatani anapita chokwawa,+ mtumiki wake akum’tsatira pambuyo. Pamenepo Yonatani+ anayamba kukantha Afilisitiwo ndipo mtumiki wake uja anali kumalizitsa kupha anthuwo m’mbuyo mwake.+ 14 Nthawi yoyamba imene Yonatani ndi mtumiki wakeyo anakantha Afilisitiwo anapha anthu 20, pamalo okwana pafupifupi hafu ya m’litali mwa ekala.*

15 Kenako anthu amene anali kutchire mumsasa ndi anthu onse kumudzi wa asilikaliwo anayamba kunjenjemera.+ Anthu olanda katundu+ nawonso anali kunjenjemera, ndipo nthaka inayamba kugwedezeka.+ Zimenezi zinali zochokera kwa Mulungu.+ 16 Alonda a Sauli ku Gibeya+ wa ku Benjamini anaona zimene zinali kuchitika, ndipo anaona kuti chipwirikiti chafalikira paliponse mumsasamo.+

17 Ndiyeno Sauli anauza anthu amene anali naye kuti: “Werengani anthu kuti muone amene wachoka.” Atawerenga anthuwo, anapeza kuti Yonatani ndi mtumiki wake womunyamulira zida palibe. 18 Pamenepo Sauli anauza Ahiya+ kuti: “Bweretsa likasa la Mulungu woona!”+ (Pakuti masiku amenewo likasa la Mulungu woona linali ndi ana a Isiraeli.)+ 19 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Sauli anali kulankhula ndi wansembe,+ chipwirikiti mumsasa wa Afilisiti chinapitiriza kuwonjezeka, ndipo chinali kukulirakulira. Kenako Sauli anauza wansembeyo kuti: “Basi, siya zimenezi.” 20 Choncho Sauli ndi anthu onse amene anali naye anasonkhana pamodzi kuti apite kukamenyana ndi Afilisiti.+ Ndiyeno anayenda mpaka kukafika kumene kunali nkhondoko, ndipo anapeza kuti aphana okhaokha ndi lupanga,+ moti chipwirikiti chake chinali chosaneneka. 21 Ndipo Aheberi amene anali atagwirizana ndi Afilisiti+ poyamba, amene anali atapita kukakhala mumsasa wa Afilisiti, nawonso anakhala kumbali ya Aisiraeli amene anali ndi Sauli ndi Yonatani. 22 Nawonso amuna onse a Isiraeli amene anali atabisala+ m’dera lamapiri la Efuraimu anamva kuti Afilisiti athawa, choncho Aisiraeliwo anayamba kuthamangitsa Afilisitiwo ndi kuwathira nkhondo. 23 Pa tsiku limenelo Yehova anapulumutsa+ Isiraeli, ndipo nkhondoyo inapitirira mpaka ku Beti-aveni.+

24 Motero amuna a Isiraeli anatopa kwambiri pa tsiku limenelo, komabe Sauli analumbirira+ anthuwo kuti: “Munthu aliyense wodya mkate dzuwa lisanalowe, komanso ndisanabwezere+ adani anga, ndi wotembereredwa!” Choncho panalibe aliyense mwa anthuwo amene anadya mkate.+

25 Ndiyeno anthu onse a m’dzikomo anapita kunkhalango, pa nthawi imene uchi+ unali pena paliponse kutchireko. 26 Anthuwo atalowa m’nkhalangomo, anaona uchi+ ukukha. Pa nthawiyi panalibe amene anadya, chifukwa anali kuopa lumbiro lija.+ 27 Koma Yonatani sanamve pamene bambo ake analumbirira anthu.+ Chotero anatambasula dzanja lake ndi kukhudza chisa cha uchi ndi ndodo. Kenako ananyambita ndodoyo, ndipo atatero, anayera m’maso.+ 28 Pamenepo mmodzi mwa anthuwo anamuuza kuti: “Bambo ako alumbirira anthu kuti, ‘Munthu aliyense wodya mkate lero ndi wotembereredwa!’”+ (Apa n’kuti anthuwo atayamba kutopa.)+ 29 Poyankha, Yonatani anati: “Bambo anga achititsa kuti dziko lonse livutike.+ Taonani mmene maso anga ayerera chifukwa ndalawa uchi pang’ono chabe.+ 30 Anthu akanadya+ zimene afunkha kwa adani awo,+ Afilisiti tikanawagonjetsa. Koma onani, sitinawakanthe mokwanira.”+

31 Choncho pa tsiku limenelo, iwo anapitiriza kupha Afilisiti kuyambira ku Mikimasi+ mpaka ku Aijaloni,+ moti anthu anatopa kwambiri.+ 32 Zitatero, anthuwo anayamba kuthamangira zofunkha mosusuka+ ndi kutenga nkhosa, ng’ombe ndi ana a ng’ombe. Zimenezi anali kuziphera pansi, ndipo anthuwo anayamba kudya nyamayo pamodzi ndi magazi ake.+ 33 Tsopano anthu anauza Sauli kuti: “Taonani! Anthu akuchimwira Yehova mwa kudya nyama pamodzi ndi magazi ake.”+ Chotero iye anati: “Mwachita zinthu mosakhulupirika. Choyamba, kunkhunizani chimwala mubwere nacho kuno.” 34 Kenako Sauli anati: “Pitani pakati pa anthu ndipo muwauze kuti, ‘Aliyense wa inu abweretse kwa ine ng’ombe yake yamphongo ndi nkhosa, ndipo mudzaziphere ndi kuzidyera pano. Musachimwire Yehova mwa kudya nyama pamodzi ndi magazi ake.’”+ Usiku umenewo, aliyense mwa anthuwo anabweretsa ng’ombe yamphongo imene anali nayo ndi kuiphera pamenepo. 35 Zitatero, Sauli anamangira Yehova guwa lansembe,+ limene linali guwa lake loyamba kumangira Yehova.+

36 Kenako Sauli anati: “Tiyeni tipite kwa Afilisiti usiku kuti tikafunkhe zinthu zawo kufikira kutacha,+ ndipo tisasiyepo ngakhale munthu mmodzi pakati pawo.”+ Anthuwo poyankha anati: “Chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino.” Ndiyeno wansembe anati: “Tiyeni tifikire Mulungu woona pamalo ano.”+ 37 Chotero Sauli anayamba kufunsira kwa Mulungu, kuti: “Kodi ndipite kwa Afilisiti?+ Kodi muwapereka m’manja mwa Isiraeli?”+ Koma Mulungu sanamuyankhe pa tsikuli.+ 38 Choncho Sauli ananena kuti: “Bwerani kuno,+ inu nonse atsogoleri a anthu,+ ndipo tifufuze ndi kudziwa mmene tchimoli lachitikira lero. 39 Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo, Mlanditsi wa Isiraeli, munthu amene wachititsa tchimoli ayenera kufa ndithu,+ ngakhale atakhala Yonatani mwana wanga.” Koma panalibe ngakhale munthu mmodzi womuyankha mwa anthu onsewo. 40 Ndiyeno anapitiriza kuuza Aisiraeli onse kuti: “Inuyo mukhale kumbali ina, ndipo ine ndi mwana wanga Yonatani tikhalanso ku mbali ina.” Pamenepo anthuwo anauza Sauli kuti: “Chitani zimene mukuona kuti n’zabwino.”+

41 Ndiyeno Sauli anauza Yehova kuti: “Mulungu wa Isiraeli inu, tiyankheni kudzera mwa Tumimu!”+ Atatero, Tumimuyo analoza kwa Yonatani ndi Sauli, ndipo anthuwo anachoka.+ 42 Kenako Sauli anati: “Chitani maere+ pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga.” Zitatero, maerewo anagwera Yonatani. 43 Tsopano Sauli anafunsa Yonatani kuti: “Ndiuze, Wachita chiyani?”+ Poyankha, Yonatani anamuuza kuti: “Zoonadi, ndalawa uchi pang’ono kunsonga ya ndodo imene ili m’manja mwangayi.+ Ndiye ndiphenitu!”

44 Pamenepo Sauli anati: “Mulungu andilange mowirikiza+ ngati suufa ndithu,+ Yonatani.” 45 Koma anthu anauza Sauli kuti: “Kodi Yonatani amene wagwira ntchito yobweretsa chipulumutso chachikulu chimenechi+ mu Isiraeli afe? Sizitheka zimenezo!+ Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ ngakhale tsitsi limodzi+ la m’mutu wake siligwa pansi, pakuti iye wachita zimenezi lero mothandizidwa ndi Mulungu.”+ Ndi mawu amenewa anthuwo anapulumutsa+ Yonatani, moti sanafe.

46 Choncho Sauli anasiya kutsatira Afilisiti, moti nawonso Afilisiti anabwerera kwawo.+

47 Tsopano Sauli analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli+ ndipo anamenya nkhondo ndi adani ake onse om’zungulira. Iye anamenyana ndi Mowabu,+ ana a Amoni,+ Edomu,+ mafumu a Zoba+ ndi Afilisiti.+ Kulikonse kumene anali kutembenukira anali kuwalanga.+ 48 Iye anapitiriza kuchita chamuna+ ndipo anapha Aamaleki+ ndi kulanditsa Isiraeli m’manja mwa wofunkha.

49 Ana aamuna a Sauli anali Yonatani,+ Isivi ndi Malikisuwa.+ Ndipo mayina a ana ake awiri aakazi ndi awa: Woyamba kubadwa anali Merabu,+ ndipo wamng’ono anali Mikala.+ 50 Mkazi wa Sauli dzina lake anali Ahinowamu, mwana wamkazi wa Ahimazi. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Abineri+ mwana wa Nera, m’bale wa bambo ake a Sauli. 51 Bambo ake a Sauli anali Kisi,+ ndipo Nera,+ bambo ake a Abineri, anali mwana wa Abiyeli.

52 M’masiku onse a Sauli, Afilisiti anali kupanikizidwa ndi nkhondo.+ Ndipo Sauli akaona munthu aliyense wamphamvu kapena wolimba mtima, anali kum’tenga kuti akhale msilikali wake.+

15 Ndiyeno Samueli anauza Sauli kuti: “Yehova anatuma ine kudzakudzoza+ kukhala mfumu ya anthu ake Aisiraeli, choncho imva zimene Yehova wanena.+ 2 Yehova wa makamu+ wanena kuti, ‘Ndibwezera+ Aamaleki chifukwa choukira Aisiraeli panjira, pamene Aisiraeliwo anali kutuluka mu Iguputo.+ 3 Tsopano pita ukaphe Aamaleki+ ndi kuwawononga+ pamodzi ndi zonse zimene ali nazo. Usakawamvere chisoni, ukawaphe ndithu. Ukaphe+ mwamuna ndi mkazi, mwana wamng’ono ndi mwana woyamwa,+ ng’ombe ndi nkhosa, ngamila ndi bulu.’”+ 4 Motero, Sauli anaitanitsa anthu ku Telayimu+ ndi kuwawerenga. Iye anapeza kuti panali amuna oyenda pansi 200,000 ndiponso amuna a ku Yuda 10,000.+

5 Kenako, Sauli anafika kumzinda wa Amaleki ndi kuubisalira kuchigwa.* 6 Zili choncho, Sauli anauza Akeni+ kuti: “Nyamukani,+ muchoke pakati pa Aamaleki kuti ndisakuwonongeni pamodzi nawo. Inuyo munasonyeza kukoma mtima kosatha kwa ana onse a Isiraeli+ atatuluka mu Iguputo.”+ Choncho Akeni anachokadi pakati pa Aamaleki. 7 Atachoka, Sauli anapha Aamaleki+ kuyambira ku Havila+ mpaka ku Shura,+ kufupi ndi Iguputo. 8 Iye anagwira Agagi+ mfumu ya Amaleki ali wamoyo, ndipo anthu ena onse anawapha ndi lupanga.+ 9 Koma Sauli ndi anthu ake anamvera chisoni Agagi ndipo sanaphe nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambiri,+ ziweto zonenepa, nkhosa zamphongo ndi zina zonse zimene zinali zabwino. Iwo sanafune kupha zimenezi,+ koma anawononga zinthu zina zonse zimene zinali zonyansa ndi zonyozeka.

10 Ndiyeno Yehova anauza Samueli kuti: 11 “Ndikumva chisoni+ kuti ndinaika Sauli kukhala mfumu. Iye watembenuka,+ wasiya kunditsatira, ndipo sakumvera mawu anga.”+ Samueli anavutika maganizo kwambiri ndi nkhani imeneyi+ moti anafuulira Yehova usiku wonse.+ 12 Kenako Samueli anadzuka m’mawa kwambiri kuti akaonane ndi Sauli. Koma uthenga unam’peza Samueli wonena kuti: “Sauli anabwera ku Karimeli,+ ndipotu waimika chipilala+ cha chikumbutso chake, kenako watembenuka ndipo wapita ku Giligala.” 13 Patapita nthawi Samueli anam’peza Sauli, ndipo Sauli anauza Samueli kuti: “Yehova akudalitseni.+ Ndachita zimene Yehova ananena.”+ 14 Koma Samueli anati: “Nanga kulira kwa nkhosa ndi ng’ombe kumene ndikumvaku kukutanthauza chiyani?”+ 15 Poyankha Sauli anati: “Anthuwa+ azitenga kwa Aamaleki, chifukwa sanaphe nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambirizi n’cholinga chofuna kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.+ Koma zina zonse zotsala taziwononga.” 16 Pamenepo Samueli anauza Sauli kuti: “Khala chete! Ndikuuza zimene Yehova walankhula nane usiku wapitawu.”+ Sauli anayankha kuti: “Lankhulani!”

17 Ndiyeno Samueli anati: “Kodi sunali kudziona ngati ndiwe mwana+ utakhala mtsogoleri wa mafuko onse a Isiraeli, pamene Yehova anakudzoza+ kuti ukhale mfumu ya Isiraeli? 18 Kenako Yehova anakutuma kuti, ‘Pita ukaphe anthu ochimwa,+ Aamaleki, ndi kumenyana nawo kufikira utawafafaniza.’+ 19 Ndiye n’chifukwa chiyani sunamvere mawu a Yehova, koma unathamangira zofunkha mosusuka+ ndi kuyamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova?”+

20 Sauli anayankha Samueli kuti: “Komatu ndamvera+ mawu a Yehova, chifukwa ndachita ntchito imene Yehova anandituma, ndipo ndabweretsa Agagi,+ mfumu ya Amaleki. Koma Aamalekiwo ndawapha.+ 21 Anthuwa+ atenga pa zofunkha, nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambiri, pa zinthu zimene zinayenera kuwonongedwa, kuti azipereke nsembe+ kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.”+

22 Poyankha Samueli anati: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza+ ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera+ kuposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kuposa mafuta+ a nkhosa zamphongo. 23 Pakuti kupanduka+ n’chimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza n’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso aterafi.+ Popeza iwe wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”+

24 Pamenepo Sauli anayankha Samueli kuti: “Ndachimwa,+ ndaphwanya lamulo la Yehova komanso sindinamvere mawu anu, chifukwa ndinaopa anthu+ ndipo ndamvera mawu awo. 25 Tsopano ndikhululukireni+ tchimo langa chonde, ndipo mubwerere nane kuti ndikagwade ndi kuweramira pansi+ pamaso pa Yehova.” 26 Samueli anamuyankha kuti: “Sindibwerera nawe chifukwa wakana mawu a Yehova, ndipo Yehova wakukana kuti upitirize kukhala mfumu ya Isiraeli.”+ 27 Pamene Samueli anali kutembenuka kuti azipita, nthawi yomweyo Sauli anagwira m’munsi mwa malaya akunja odula manja a Samueli, koma malayawo anang’ambika.+ 28 Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wang’amba+ ndi kuchotsa ufumu wa Isiraeli kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa mnzako, munthu woyenerera kuposa iwe.+ 29 Kuwonjezera apo, Wolemekezeka wa Isiraeli+ sadzalephera kukwaniritsa mawu ake,+ ndipo sadzadzimva kuti ali ndi mlandu, pakuti Iye si munthu kuti adzimve wamlandu.”+

30 Pamenepo Sauli anati: “Ndachimwa. Komabe, ndilemekezeni+ chonde pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Isiraeli. Mubwerere nane ndipo ndidzagwada ndi kuweramira pansi pamaso pa Yehova Mulungu wanu.”+ 31 Choncho Samueli anabwerera akuyenda pambuyo pa Sauli. Ndipo Sauli anagwada ndi kuweramira pansi pamaso pa Yehova. 32 Kenako Samueli anati: “M’bweretseni kuno Agagi mfumu ya Amaleki.” Atatero, Agagi anapita kwa Samueli mwamantha ndi mokayikira.* Mumtima mwake Agagi anayamba kunena kuti: “Ndithudi, ululu wa imfa wachoka.” 33 Koma Samueli anati: “Monga mmene akazi anaferedwera ana awo chifukwa cha lupanga lako,+ momwemonso mayi ako+ aferedwa ana koposa akazi onse.”+ Pamenepo Samueli anadula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.+

34 Tsopano Samueli ananyamuka kupita ku Rama, koma Sauli anapita kunyumba kwake ku Gibeya.+ 35 Samueli analirira+ Sauli ndipo sanaonanenso naye mpaka tsiku la imfa yake. Koma Yehova anamva chisoni kuti anaika Sauli kukhala mfumu ya Isiraeli.+

16 Patapita nthawi, Yehova anauza Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli+ mpaka liti, pamene ine ndamukana kuti alamulire monga mfumu ya Isiraeli?+ Thira mafuta m’nyanga yako+ ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese+ wa ku Betelehemu, chifukwa ndapeza munthu pakati pa ana ake aamuna woti akhale mfumu yanga.”+ 2 Koma Samueli anati: “Ndipita bwanji? Sauli akangomva andipha ndithu.”+ Atatero, Yehova anamuuza kuti: “Popita utenge ng’ombe yaikazi yaing’ono pakati pa ng’ombe zako, ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova.’+ 3 Ukakatero ukaitanire Jese kopereka nsembeko, ndipo ine ndidzakuuza zochita.+ Kumeneko ukandidzozere+ munthu amene ndidzakusonyeza.”

4 Samueli anachita zimene Yehova anamuuza. Atafika ku Betelehemu,+ akulu a mzindawo anayamba kunjenjemera+ atakumana naye. Ndiyeno iwo anati: “Kodi n’kwabwino?”+ 5 Iye anayankha kuti: “Inde, n’kwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Dziyeretseni,+ ndipo mupite nane kopereka nsembe.” Chotero iye anayeretsa Jese ndi ana ake, kenako anawaitanira kopereka nsembe. 6 Tsopano zimene zinachitika n’zakuti, pamene iwo anali kulowa, ndipo Samueli ataona Eliyabu,+ nthawi yomweyo anati: “Mosakayikira wodzozedwa wake waonekera pamaso pa Yehova.” 7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake,+ pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.+ Munthu amaona zooneka ndi maso,+ koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”+ 8 Pamenepo, Jese anaitana Abinadabu+ kuti adutse pamaso pa Samueli, koma Samueli anati: “Yehova sanasankhenso ameneyu.” 9 Kenako Jese anaitana Shama+ kuti adutse, koma Samueli anati: “Yehova sanasankhenso ameneyu.” 10 Choncho Jese anadutsitsa ana ake 7 pamaso pa Samueli. Koma Samueli anauza Jese kuti: “Yehova sanasankhe aliyense mwa amenewa.”

11 Pamapeto pake Samueli anafunsa Jese kuti: “Kodi anyamata ako onse ndi omwewa basi?” Iye anayankha kuti: “Wamng’ono kwambiri sanabwerebe,+ pakuti akuweta nkhosa.”+ Chotero Samueli anauza Jese kuti: “Tumiza munthu akam’tenge, chifukwa sitikhala pansi kuti tidye kufikira iye atabwera pano.” 12 Iye anatumadi munthu kukam’tenga. Mnyamatayo anali wamaonekedwe ofiirira,+ mnyamata wa maso okongola, ndiponso wooneka bwino. Pamenepo Yehova anati: “Ndi ameneyu! Nyamuka umudzoze.”+ 13 Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.+ Kenako Samueli ananyamuka kupita ku Rama.+

14 Tsopano mzimu wa Yehova unachoka+ pa Sauli, ndipo Yehova analola maganizo oipa*+ kum’vutitsa Sauli. 15 Zitatero, atumiki a Sauli anayamba kumuuza kuti: “Taonani tsopano, mzimu woipa wa Mulungu ukukuvutitsani. 16 Mbuye wathu, chonde, lamulani kuti atumiki anu amene ali pamaso panu akufunireni katswiri+ woimba zeze.+ Ndiyeno mzimu woipa wa Mulungu ukabwera pa inu, iye azikuimbirani zezeyo, ndipo inu muzipeza bwino.” 17 Chotero Sauli anauza atumiki ake kuti: “Chonde, ndipezereni munthu wodziwa kuimba, ndipo mubwere naye kuno.”+

18 Mmodzi mwa atumikiwo anayankha, kuti: “Inetu ndinaona luso loimba+ la mwana wa Jese wa ku Betelehemu. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso wamphamvu,+ mwamuna wankhondo,+ wolankhula mwanzeru+ ndi wooneka bwino,+ komanso Yehova ali naye.”+ 19 Atamva zimenezi, Sauli anatuma mithenga kwa Jese, kuti: “Nditumizire mwana wako Davide amene akuweta nkhosa.”+ 20 Pamenepo Jese anatenga bulu, mkate, thumba lachikopa+ la vinyo ndi mwana wa mbuzi, ndipo anazitumiza kwa Sauli kudzera mwa Davide mwana wake.+ 21 Choncho Davide anapita kwa Sauli ndipo anali kum’tumikira.+ Sauli anam’konda kwambiri Davide, moti anakhala womunyamulira zida zake.+ 22 Zitatero, Sauli anatumiza uthenga kwa Jese, kuti: “Chonde, lola kuti Davide apitirize kunditumikira, chifukwa ndam’konda.” 23 Ndiyeno mzimu woipa wa Mulungu ukafika pa Sauli, Davide anali kutenga zeze ndi kumuimbira. Akatero, Sauli anali kupeza bwino, ndipo mzimu woipawo unali kum’chokera.+

17 Ndiyeno Afilisiti+ anayamba kusonkhanitsa anthu a m’misasa yawo kuti akamenye nkhondo. Atasonkhana pamodzi ku Soko,+ m’dera la Yuda, anakamanga msasa pakati pa Soko ndi Azeka+ ku Efesi-damimu.+ 2 Koma Sauli ndi amuna a Isiraeli anasonkhana pamodzi n’kumanga msasa m’chigwa cha Ela,+ ndipo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi Afilisiti. 3 Afilisitiwo anaimirira paphiri kumbali ina, ndipo Aisiraeli anaimirira paphiri kumbali inanso. Pakati pawo panali chigwa.

4 Ndiyeno kumsasa wa Afilisiti kunatuluka ngwazi, dzina lake Goliyati,+ wa ku Gati.+ Iye anali wamtali mikono 6 ndi chikhatho chimodzi.*+ 5 Anali atavala chisoti chamkuwa kumutu kwake ndi chovala chamamba achitsulo. Mkuwa wa chovala chamamba chimenecho+ unali wolemera masekeli* 5,000. 6 Mwamunayu anali atavalanso zoteteza miyendo zamkuwa ndipo anali atanyamula nthungo*+ yamkuwa kumsana kwake. 7 Mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu,+ ndipo mutu wachitsulo wa mkondowo unali wolemera masekeli 600. Munthu womunyamulira chishango chake chachikulu anali kuyenda patsogolo pake. 8 Choncho iye anaima n’kuyamba kufuulira asilikali a Isiraeli+ kuti: “N’chifukwa chiyani mukufola mwa dongosolo lomenyera nkhondo? Ine ndabwera kudzamenyera nkhondo Afilisiti. Inuyo ndinu antchito+ a Sauli. Ndiye sankhani munthu woti amenyane nane, ndipo abwere kuno. 9 Ngati angathe kumenyana nane n’kundipha, ndiye kuti tidzakhala antchito anu. Koma ngati ndingalimbane naye mpaka kumupha, inuyo mudzakhala antchito athu, ndipo muzititumikira.”+ 10 Ndiyeno Mfilisiti uja anapitiriza kunena kuti: “Ine ndikutonza+ asilikali a Isiraeli lero. Ndipatseni mwamuna woti ndimenyane naye!”+

11 Sauli+ ndi Aisiraeli onse atamva mawu a Mfilisitiwa anaopsezedwa ndipo anachita mantha kwambiri.+

12 Tsopano Davide anali mwana wamwamuna wa Jese, Mwefurata+ wina wa ku Betelehemu, ku Yuda. Jese anali ndi ana aamuna 8+ ndipo m’masiku a Sauli iye anali atakalamba kale. 13 Ndiyeno ana atatu aakulu a Jese anatsatira Sauli kunkhondo.+ Mayina a ana ake atatu amene anapita kunkhondowo anali Eliyabu,+ woyamba kubadwa, Abinadabu+ mwana wake wachiwiri, ndi Shama,+ wachitatu. 14 Davide anali wamng’ono kwambiri pa ana onse aamuna,+ ndipo ana atatu aakulu a Jese anatsatira Sauli.

15 Davide anali kupita kwa Sauli ndi kubwerera ku Betelehemu kukaweta nkhosa+ za bambo ake. 16 Kwa masiku 40, Mfilisiti uja anali kubwera m’mawa kwambiri ndi madzulo kudzadzionetsera.

17 Kenako Jese anauza Davide mwana wake kuti: “Tenga tirigu wokazinga+ uyu wokwana muyezo umodzi wa efa ndi mitanda ya mkate 10, upite nazo mofulumira kwa abale ako kumsasa. 18 Magawo 10 awa a mkaka* ukapatse mtsogoleri wa gulu la anthu 1,000.+ Ukafufuzenso kuti abale ako ali bwanji,+ ndipo akakupatse chizindikiro chosonyeza kuti ali bwino.” 19 Pa nthawiyi, Sauli, ana a Jese ndi amuna ena onse a Isiraeli anali m’chigwa cha Ela+ kuti amenyane ndi Afilisiti.+

20 Choncho Davide anadzuka m’mawa kwambiri, atasiya nkhosa zake m’manja mwa wozisamalira. Iye ananyamula katundu wake ndi kunyamuka monga mmene Jese, bambo ake, anamuuzira.+ Atafika mkati mwa mpanda wa msasa,+ anapeza asilikali akupita kumalo omenyera nkhondo,+ akufuula mfuwu ya nkhondo. 21 Pamenepo asilikali a Isiraeli ndi asilikali a Afilisiti anafola kuti akumane. 22 Nthawi yomweyo, Davide anasiya katundu+ wake m’manja mwa munthu wosamalira katundu,+ ndipo anathamangira kumalo omenyera nkhondo. Atafika kumeneko, anayamba kufunsa za abale ake ngati ali bwino.+

23 Pamene anali kulankhula ndi asilikaliwo, anangoona ngwazi ija yatulukira kuchokera pakati pa asilikali a Afilisiti. Dzina la ngwaziyo linali Goliyati,+ Mfilisiti wa ku Gati.+ Iye anayamba kulankhula mawu omwe aja amene analankhula poyamba,+ moti Davide anamva nawo. 24 Koma amuna onse a Isiraeli atangoona mwamunayu anayamba kuthawa, chifukwa anachita naye mantha kwambiri.+ 25 Pamenepo amuna a Isiraeli anayamba kunena kuti: “Mukumuona mwamuna amene akubwerayu? Iye akubwera kudzatonza+ Isiraeli. Munthu amene angamukanthe ndi kumupha, mfumu idzam’patsa chuma chochuluka ndi kum’patsanso mwana wake wamkazi.+ Komanso, mfumu idzamasula nyumba ya bambo ake a munthuyo kuti isamapereke chilichonse mwa zinthu zimene Aisiraeli ayenera kupereka kwa mfumu.”+

26 Ndiyeno Davide anayamba kufunsa amuna amene anali ataimirira pafupi naye kuti: “Kodi munthu amene angakaphe Mfilisiti+ ameneyu ndi kuchotsa chitonzo pa Isiraeli+ amuchitira chiyani? Kodi Mfilisiti wosadulidwa+ ameneyu ndani kuti azinyoza+ asilikali a Mulungu wamoyo?”+ 27 Ndiyeno anthu anamuuzanso mawu amene anamuuza poyamba aja, kuti: “Munthu amene angaphe Mfilisiti ameneyu am’chitira zimenezi.” 28 Tsopano Eliyabu,+ m’bale wake wamkulu kwambiri wa Davide anamva zimene Davideyo anali kulankhula ndi amunawo. Eliyabu anapsa mtima kwambiri chifukwa cha Davide,+ moti anati: “N’chifukwa chiyani wabwera kuno? Nanga nkhosa zochepa za bambo wasiyira ndani kuchipululu?+ Ine ndikudziwa bwino kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako,+ chifukwa wabwera kuno kuti udzaonerere nkhondo.”+ 29 Poyankha Davide anati: “Tsopano ndachita chiyani? Inetu ndangofunsa chabe.”+ 30 Atatero, anatembenuka ndi kum’chokera kupita kwa munthu wina. Kwa munthu ameneyu anafunsanso funso lomwe lija,+ ndipo anthu anamuyankhanso chimodzimodzi ngati poyamba paja.+

31 Anthu anamva zimene Davide ananena, ndipo anapita kukauza Sauli. Choncho Sauli anamuitanitsa. 32 Davide anauza Sauli kuti: “Musalole kuti aliyense agwidwe ndi mantha mumtima mwake.+ Ine mtumiki wanu ndipita kukamenyana ndi Mfilisiti ameneyu.”+ 33 Koma Sauli anauza Davide kuti: “Sungapite kukamenyana ndi Mfilisiti ameneyu,+ chifukwa ndiwe mwana,+ ndipo Mfilisiti ameneyu wakhala akumenya nkhondo kuyambira ubwana wake.” 34 Davide anauza Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala m’busa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwera mkango+ komanso chimbalangondo moti chilichonse mwa zilombo zimenezi chinagwira nkhosa ya m’gululo. 35 Pamenepo ine ndinatsatira chilombocho n’kuchipha,+ ndipo ndinapulumutsa nkhosa m’kamwa mwake. Chitayamba kundiukira, ndinagwira ndevu zake, n’kuchikantha ndi kuchipha. 36 Mtumiki wanu anapha zonse ziwiri, mkangowo ndi chimbalangondocho. Mfilisiti wosadulidwayu+ akhalanso ngati chimodzi mwa zilombo zimenezi, chifukwa watonza+ asilikali+ a Mulungu wamoyo.”+ 37 Ndiyeno Davide anawonjezera kuti: “Yehova amene anandilanditsa m’kamwa mwa mkango ndi m’kamwa mwa chimbalangondo andilanditsanso m’manja mwa Mfilisiti ameneyu.”+ Pamenepo Sauli anauza Davide kuti: “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.”+

38 Tsopano Sauli anayamba kuveka Davide zovala zake. Anamuveka chisoti chamkuwa kumutu kwake, komanso chovala chamamba achitsulo. 39 Kenako Davide anamangirira lupanga pazovala zake. Pamene anafuna kunyamuka, iye analephera kuyenda chifukwa zovalazo sanazizolowere. Ndiyeno Davide anauza Sauli kuti: “Sinditha kuyenda nazo zovala zimenezi chifukwa sindinazizolowere.” Atatero, Davide anavula zovalazo.+ 40 Ndiyeno anatenga ndodo m’manja mwake ndi kusankha miyala isanu yosalala kwambiri ya m’chigwa.* Iye anaika miyalayi m’chikwama chake cha kubusa mmene anali kusungiramo zinthu, ndipo m’manja mwake munali gulaye.*+ Kenako anayamba kupita kumene kunali Mfilisiti uja.

41 Mfilisiti uja anayamba kupita kumene kunali Davide, ndipo anali kumuyandikirabe. Patsogolo pake panali munthu amene anali kumunyamulira chishango chake chachikulu. 42 Mfilisitiyo ataona Davide, anayamba kumuderera+ chifukwa anali mnyamata+ wamaonekedwe ofiirira,+ ndiponso wokongola.+ 43 Choncho iye anafunsa Davide kuti: “Kodi ine ndine galu+ kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Atatero, anatemberera Davide m’dzina la milungu yake.+ 44 Iye anapitiriza kuuza Davide kuti: “Tangoyerekeza kubwera kuno, ndipereka mnofu wako kwa mbalame zam’mlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire.”+

45 Poyankha Davide anauza Mfilisitiyo kuti: “Iwe ukubwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo,+ koma ine ndikubwera kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu,+ Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wam’tonza.+ 46 Lero Yehova akupereka m’manja mwanga,+ ndipo ndikupha ndi kukudula mutu. Lero ndipereka mitembo ya anthu a m’misasa ya Afilisiti kwa mbalame zam’mlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire.+ Anthu onse a padziko lapansi adzadziwa kuti Isiraeli ali ndi Mulungu.+ 47 Ndipo mpingo wonsewu udziwa kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo,+ chifukwa Yehova ndiye mwini nkhondo,+ moti apereka anthu inu m’manja mwathu.”+

48 Ndiyeno zinachitika kuti Mfilisiti uja anayamba kuyenda, kuyandikira Davide. Nayenso Davide anayamba kuyenda mofulumira ndi kuthamangira kumalo omenyera nkhondo kuti akakumane naye.+ 49 Pamenepo Davide anapisa dzanja m’chikwama chake ndi kutengamo mwala. Kenako anauponya ndi gulaye moti unamenya+ Mfilisiti uja pamphumi n’kuloweratu m’mutu mwake, ndipo anagwa pansi chafufumimba.+ 50 Choncho Davide, mwa kugwiritsa ntchito gulaye ndi mwala, anali wamphamvu kuposa Mfilisiti. Iye anamukantha ndi kumupha, ndipo m’manja mwa Davide munalibe lupanga.+ 51 Pamenepo Davide anapitiriza kuthamanga ndipo anakaima pambali pake. Kenako anatenga lupanga la Mfilisitiyo,+ kulisolola m’chimake ndi kum’pheratu mwa kum’dula mutu.+ Afilisiti ena onse ataona kuti ngwazi yawo yamphamvu ija yafa, anayamba kuthawa.+

52 Zitatero, amuna a Isiraeli ndi Yuda anayamba kufuula ndi kuthamangitsa+ Afilisiti kukafika kuchigwa,+ mpaka kuzipata za mzinda wa Ekironi.+ Afilisiti amene anavulazidwa mosachiritsika anali kugwa m’njira yochokera ku Saaraimu,+ moti mitembo yawo inali paliponse mpaka kumizinda ya Gati ndi Ekironi. 53 Kenako ana a Isiraeli anasiya kuthamangitsa Afilisiti ndipo anabwerera n’kukafunkha+ zinthu za m’misasa yawo.

54 Kenako Davide anatenga mutu+ wa Mfilisiti uja ndi kupita nawo ku Yerusalemu, ndipo zida za Mfilisiti uja anaziika muhema wake.+

55 Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisiti uja, anafunsa Abineri,+ mkulu wa asilikali, kuti: “Kodi ameneyu ndi mwana+ wa ndani,+ Abineri?” Poyankha Abineri anati: “Ndikulumbira pali moyo wanu mfumu, ine sindikudziwa ngakhale pang’ono!” 56 Choncho mfumuyo inati: “Ufufuze kuti mnyamata ameneyu ndi mwana wa ndani.” 57 Chotero Davide atangofika kuchokera kumene anapha Mfilisiti, Abineri anam’tenga ndi kupita naye kwa Sauli, ali ndi mutu+ wa Mfilisiti uja m’manja mwake. 58 Ndiyeno Sauli anamufunsa kuti: “Mnyamata iwe, bambo wako ndani?” Poyankha Davide anati: “Ndine mwana wa mtumiki wanu Jese,+ wa ku Betelehemu.”+

18 Ndiyeno Davide atangomaliza kulankhula ndi Sauli, Yonatani+ anagwirizana kwambiri+ ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.+ 2 Tsiku limenelo Sauli anatenga Davide, ndipo sanamulole kubwerera kunyumba ya bambo ake.+ 3 Yonatani ndi Davide anachita pangano,+ chifukwa Yonatani anali kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera.+ 4 Pamenepo Yonatani anavula malaya ake akunja odula manja ndi kupatsa Davide. Anam’patsanso zovala zina ngakhalenso lupanga, uta ndi lamba wake. 5 Choncho Davide anayamba kupita kunkhondo. Kulikonse kumene Sauli wamutumiza anali kuchita zinthu mwanzeru,+ moti Sauli anamuika kukhala woyang’anira asilikali.+ Zimenezi zinasangalatsa anthu onse komanso atumiki a Sauli.

6 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene asilikali anali kubwerera, Davide atakantha Mfilisiti uja, akazi anayamba kutuluka m’mizinda yonse ya Isiraeli akuimba nyimbo+ ndi kuvina. Iwo anali kupita kukachingamira mfumu Sauli mosangalala,+ akuimba maseche+ komanso choimbira cha zingwe zitatu. 7 Akazi amene anali kusangalalawo anali kuimba molandizana mawu kuti:

“Sauli wakantha adani ake masauzande,

Ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi.”+

8 Sauli atamva zimenezi anakwiya kwambiri+ ndipo mawu amenewa anamuipira, moti anayamba kuganiza kuti: “Davide amupatsa masauzande makumimakumi, koma ine angondipatsa masauzande okha. Ndiye kuti kwangotsala kum’patsa ufumuwu basi!”+ 9 Kuyambira tsiku limenelo, Sauli anayamba kuyang’ana Davide ndi diso loipa.+

10 Tsiku lotsatira,+ mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa Sauli,+ moti anayamba kuchita zinthu ngati mneneri+ m’nyumba mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kuimba nyimbo+ ngati kale ndipo Sauli anali ndi mkondo m’manja mwake.+ 11 Ndiyeno Sauli anaponya mkondo uja+ ndi kunena kuti: “Ndilasa Davide ndi kumukhomerera kukhoma* ndi mkondowu!”+ Koma Davide anamuthawa, ndipo zimenezi zinachitika kawiri konse.+ 12 Zitatero, Sauli anachita mantha+ ndi Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo,+ koma Sauliyo anali atam’chokera.+ 13 Chotero Sauli anachotsa Davide kuti asamakhale naye pafupi,+ ndipo anamuika kukhala mtsogoleri wa gulu la asilikali 1,000, moti Davide anali kutsogolera asilikali amenewo.+ 14 Davide anali kuchita zinthu mwanzeru+ nthawi zonse m’njira zake zonse, ndipo Yehova anali naye.+ 15 Sauli nayenso anali kuona kuti Davide akuchita zinthu mwanzeru,+ moti anali kuchita naye mantha. 16 Anthu onse a mu Isiraeli ndi Yuda anali kum’konda Davide, chifukwa iye anali kuwatsogolera.

17 Ndiyeno Sauli anauza Davide kuti: “Mwana wanga wamkazi wamkulu Merabu+ alipo. Ndidzakupatsa ameneyu kuti akhale mkazi wako.+ Koma iwe undisonyeze kulimba mtima kwako ndi kumenya nkhondo za Yehova.”+ Mumtima mwake Sauli anati: “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisiti.”+ 18 Koma Davide anayankha Sauli kuti: “Ndine yani ine, ndipo abale anga, anthu a m’banja la bambo anga ndani mu Isiraeli monse muno kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?”+ 19 Ndiyeno itafika nthawi yopereka Merabu mwana wamkazi wa Sauli kwa Davide, anali atam’pereka kale kwa Adiriyeli+ Mmeholati+ kuti akhale mkazi wake.

20 Tsopano Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anali kukonda Davide, ndipo anthu anauza Sauli zimenezi. Sauli atamva nkhani imeneyi anasangalala. 21 Chotero Sauli anati: “Ndidzam’patsa Mikala kuti akhale msampha kwa iye,+ ndi kuti Afilisiti amuphe.” Zitatero Sauli anauza Davide kuti: “Lero uchite nane mgwirizano wa ukwati mwa kutenga mmodzi mwa akazi awiriwa.” 22 Kuwonjezera pamenepo, Sauli analamula atumiki ake kuti: “Mukalankhule ndi Davide mwachinsinsi kuti, ‘Mfumutu ikusangalala nawe, ndipo atumiki ake onse akukonda kwambiri. Ndiye chita mgwirizano wa ukwati ndi mfumu.’” 23 Atumiki a Sauli anapita kukauza Davide mawu amenewa, koma Davide anawayankha kuti: “Kodi mukuona ngati ndi nkhani yaing’ono kuchita mgwirizano wa ukwati ndi mfumu, pamene ine ndine munthu wosauka+ ndi wonyozeka?”+ 24 Ndiyeno atumikiwo anauza Sauli kuti: “Izi n’zimene Davide anatiyankha.”

25 Pamenepo Sauli anati: “Amuna inu, mukauze Davide kuti, ‘Sikuti mfumu ikufuna ndalama za ukwati,+ koma ikufuna makungu 100 akunsonga + a Afilisiti, kuti ibwezere+ adani ake.’” Koma Sauli anali atakonza chiwembu kuti Davide aphedwe ndi Afilisiti. 26 Choncho atumiki a Sauliwo anauza Davide uthengawo, ndipo Davide anavomera kuchita mgwirizano wa ukwati+ ndi mfumu. Masiku oti apereke makunguwo kwa mfumuyo asanathe, 27 Davide pamodzi ndi asilikali ake ananyamuka, ndipo anakapha+ amuna 200 achifilisiti. Ndiyeno Davide anabwerako atatenga makungu awo a kunsonga,+ ndipo makungu onsewo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Pamenepo Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi, kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+ 28 Sauli anaona ndi kudziwa kuti Yehova ali ndi Davide.+ Ndipo Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, anam’konda kwambiri Davide.+ 29 Apanso Sauli anachita mantha kwambiri ndi Davide, moti anali kudana ndi Davide nthawi zonse.+

30 Ndiyeno akalonga+ a Afilisiti akatuluka kudzamenya nkhondo, Davide anali kuchita zinthu mwanzeru kwambiri+ mwa atumiki onse a Sauli, moti dzina la Davide linatchuka kwambiri.+

19 Patapita nthawi, Sauli anauza mwana wake Yonatani ndi atumiki ake onse kuti akufuna kupha Davide.+ 2 Koma Yonatani, mwana wa Sauli, anali kukonda kwambiri Davide.+ Choncho Yonatani anauza Davide kuti: “Sauli, bambo anga, akufuna kukupha. Chonde, mawa m’mawa ukhale wosamala. Ukakhale pamalo obisika ndipo ukabisalebe choncho.+ 3 Ine ndipita nawo kutchire kumene ukabisaleko ndipo ndikaima pafupi ndi bambo anga. Bambo anga ndilankhula nawo za iwe, ndipo ndionetsetsa zimene zichitike. Zilizonse zimene ndaonazo ndidzakuuza, sindilephera.”+

4 Chotero Yonatani analankhula zabwino+ za Davide kwa Sauli bambo ake, kuti: “Mfumu isachimwire+ mtumiki wake Davide, chifukwa iye sanakuchimwireni, ndipo wakhala akukuchitirani zinthu zabwino kwambiri.+ 5 Iye anaika moyo wake pangozi*+ n’kupha Mfilisiti uja,+ moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu+ kwa Aisiraeli onse. Inuyo munaona zimenezi zikuchitika, ndipo munasangalala. Ndiye n’chifukwa chiyani mukufuna kuchimwira magazi osalakwa, mwa kupha Davide+ popanda chifukwa?”+ 6 Sauli anamvera mawu a Yonatani, ndipo analumbira kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ Davide saphedwa.” 7 Pambuyo pake, Yonatani anaitana Davide ndi kumuuza mawu onsewa. Kenako, Yonatani anatenga Davide ndi kupita naye kwa Sauli, moti Davide anapitiriza kukhala ndi Sauli monga kale.+

8 Patapita nthawi, nkhondo inayambanso ndi Afilisiti. Davide anapita kukamenya nkhondoyo ndipo anakantha ndi kupha Afilisiti ochuluka,+ moti Afilisitiwo anathawa pamaso pake.+

9 Ndiyeno mzimu woipa wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa Sauli ali m’nyumba mwake, atatenga mkondo m’manja mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kumuimbira nyimbo. 10 Zitatero, Sauli anafuna kulasa Davide kuti amukhomerere kukhoma ndi mkondo.+ Koma Davide anaulewa+ pamaso pa Sauli, moti mkondowo unalasa khoma. Pamenepo, Davide anathawa kuti adzipulumutse usiku umenewo.+ 11 Kenako Sauli anatumiza amithenga+ kunyumba ya Davide kuti akaizungulire ndi kupha Davide m’mawa mwa tsiku limenelo.+ Koma Mikala mkazi wa Davide anauza Davideyo kuti: “Ngati supulumutsa moyo wako usiku uno, mawa ukhala utaphedwa.” 12 Nthawi yomweyo, Mikala anathandiza Davide kutulukira pawindo kuti athawe ndi kupulumuka.+ 13 Ndiyeno Mikala anatenga fano la terafi+ n’kuliika pabedi. Iye anaika ukonde waubweya wa mbuzi pamene Davide anali kutsamiritsa mutu wake, kenako anafunditsa fanolo ndi chovala.

14 Tsopano Sauli anatuma amithenga kuti akagwire Davide, koma Mikala anati: “Akudwala.”+ 15 Choncho Sauli anatuma amithengawo kuti akaone Davide, ndipo anawauza kuti: “Mubwere naye kuno pabedi lakelo kuti adzaphedwe.”+ 16 Amithengawo atalowa, anangopeza fano la terafi lili pabedi, ukonde waubweya wa mbuzi uli pamene Davide anali kutsamiritsa mutu wake. 17 Zitatero Sauli anauza Mikala kuti: “N’chifukwa chiyani wandipusitsa+ chotere mwa kuthawitsa mdani wanga+ kuti apulumuke?” Poyankha, Mikala anauza Sauli kuti: “Iyeyo anandiuza kuti, ‘Ndilole ndipite! Apo ayi, ndikupha.’”

18 Choncho Davide anathawa ndi kupulumuka,+ moti anafika kwa Samueli ku Rama.+ Atafika kumeneko anasimbira Samueli zonse zimene Sauli anam’chitira. Kenako Davide ndi Samueli anachoka ndi kupita kukakhala ku Nayoti.+ 19 Patapita nthawi, uthenga unam’peza Sauli wonena kuti: “Davide alitu ku Nayoti, ku Rama.” 20 Nthawi yomweyo, Sauli anatumiza amithenga kuti akagwire Davide. Amithengawo ataona aneneri achikulire akunenera, Samueli ataima pakati pawo kuwatsogolera, mzimu+ wa Mulungu unafika pa amithenga a Sauli aja, ndipo nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri.+

21 Sauli atamuuza zimenezi, nthawi yomweyo anatumiza amithenga ena, ndipo nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. Zitatero, Sauli anatumiza amithenga enanso, gulu lachitatu, koma amenewanso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. 22 Pamapeto pake, Sauli nayenso anapita ku Rama. Atafika pachitsime chachikulu chimene chili ku Seku, anayamba kufunsa kuti: “Kodi Samueli ndi Davide ali kuti?” Poyankha, iwo anati: “Iwo ali ku Nayoti,+ ku Rama.” 23 Pamenepo anapitiriza ulendo wake wopita ku Nayoti, ku Rama, ndipo mzimu+ wa Mulungu unafika ngakhalenso pa iye. Zitatero, iye anapitiriza kuyenda ndi kuchita zinthu ngati mneneri mpaka kukafika ku Nayoti, ku Rama. 24 Sauli nayenso anavula zovala zake, ndipo nayenso anayamba kuchita zinthu ngati mneneri pamaso pa Samueli. Iye anagwa pansi ndi kugona pomwepo ali wosavala* usana wonse ndi usiku wonse.+ N’chifukwa chake pali mawu okuluwika akuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mmodzi wa aneneri?”+

20 Ndiyeno Davide anathawa+ kuchoka ku Nayoti, ku Rama. Koma anapita kwa Yonatani ndi kumuuza kuti: “Kodi ine ndachita chiyani?+ Ndalakwanji, ndipo bambo ako ndawachimwira chiyani kuti azindifunafuna kuti andiphe?” 2 Pamenepo Yonatani anamuyankha kuti: “N’zosatheka zimenezo,+ suufa. Bambo anga sangachite chilichonse chachikulu kapena chaching’ono osandiuza ine.+ Ndiye bambo anga angandibisire nkhani imeneyi chifukwa chiyani?+ Sizingachitike zimenezo.” 3 Koma poyankha Davide analumbira+ kuti: “Bambo ako ayenera kuti akudziwa ndithu kuti iweyo umandikonda.+ Pa chifukwa chimenechi iwo adzanena kuti, ‘Musamuuze zimenezi Yonatani kuti zingamupweteketse mtima.’ Moti ndikunenetsa, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wako,+ imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!”+

4 Ndiyeno Yonatani anauza Davide kuti: “Ine ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene.” 5 Poyankha, Davide anauza Yonatani kuti: “Mawatu ndi tsiku lokhala mwezi,+ ndipo mosalephera ndiyenera kukadya pamodzi ndi mfumu. Ndiyeno iweyo undilole ndipite kuti ndikabisale+ kutchire mpaka mkuja madzulo. 6 Ngati bambo ako angafunse za ine, uwauze kuti, ‘Davide anandichonderera kuti ndimulole kuchoka kuti athamangire kumzinda wakwawo ku Betelehemu,+ chifukwa banja lawo lonse likukapereka nsembe ya pachaka.’+ 7 Ngati anganene kuti, ‘Palibe vuto!’ ndiye kuti zinthu zili bwino kwa mtumiki wako. Koma ngati angakwiye, udziwe kuti atsimikiza mtima kuchita kenakake koipa.+ 8 Ukatero undisonyeze kukoma mtima kosatha ine mtumiki wako,+ pakuti unandilowetsa m’pangano+ la Yehova pamodzi ndi iwe. Koma ngati ndili wolakwa,+ undiphe ndiwe, m’malo moti uchite kukandipereka kwa bambo ako.”

9 Pamenepo Yonatani anati: “N’zosatheka kuti iwe ukhale wolakwa! Koma ngati ndingadziwe zoipa zimene bambo anga akufuna kukuchitira, ukuganiza kuti sindingakuuze?”+ 10 Ndiyeno Davide anauza Yonatani kuti: “Nanga adzandiuza ndani ngati bambo ako akuyankha mwaukali?” 11 Poyankha, Yonatani anauza Davide kuti: “Tiye kuno, tipite kutchire.” Choncho onse awiri anapita kuthengo. 12 Yonatani anauzanso Davide kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli+ akhale mboni,+ ndidzalankhula ndi bambo anga mawa kapena mkuja, ndipo ngati alibe chifukwa ndi iwe Davide, ndithu ine ndikutumizira uthenga wokudziwitsa zimenezi. 13 Yehova andilange ine Yonatani mowirikiza,+ ndikadziwa kuti bambo anga akufuna kukuchitira choipa koma osakudziwitsa ndi kukulola kuti uchoke, moti iweyo n’kulepheradi kuchoka mwamtendere. Yehova akhale nawe+ monga mmene anakhalira ndi bambo anga.+ 14 Ndipo ine ndikadzakhalabe ndi moyo,+ kodi sudzandisonyeza kukoma mtima kosatha kwa Yehova kuti ndisafe?+ Kodi sudzatero? 15 Chonde, usadzasiye kusonyeza nyumba yanga kukoma mtima kosatha mpaka kalekale.+ Ngakhalenso pamene Yehova adzawononga mdani aliyense wa Davide padziko lapansi, 16 dzina la Yonatani lisadzadulidwe m’nyumba ya Davide.+ Yehova adzaimbe mlandu adani a Davide, pangano limeneli likadzasweka.” 17 Choncho Yonatani analumbiranso kwa Davide chifukwa chakuti anali kum’konda kwambiri. Pakuti Yonatani anali kukonda Davide monga mmene anali kudzikondera iye mwini.+

18 Ndiyeno Yonatani anapitiriza kunena kuti: “Mawa ndi tsiku lokhala mwezi,+ ndipo tidzakusowa, chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu. 19 Ndipo mkuja tidzakusowanso kwambiri. Pa tsiku logwira ntchito, iweyo udzabwere pamalo amene unabisala,+ ndipo udzakhale pafupi ndi mwala uwu. 20 Ineyo ndidzaponya mivi itatu kumbali ina ya mwalawo, kuilunjikitsa pachinachake. 21 Ndiyeno ndidzatumiza mtumiki kuti, ‘Pita ukatole miviyo.’ Koma mtumikiyo ndikadzamuuza mawu akuti, ‘Mivi ili kumbali yakutiyakuti, pita ukatole,’ iweyo ukatuluke chifukwa ndiye kuti zinthu zili bwino ndipo palibe chodetsa nkhawa chilichonse. Ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo.+ 22 Koma mnyamatayo ndikadzamuuza kuti, ‘Mivi ili kutali kwambiri ndi iwe,’ ndiye kuti uyenera kuchoka, chifukwa Yehova wakulola kupita. 23 Yehova akhale mboni yathu mpaka kalekale,+ pa mawu awa amene tauzana+ ine ndi iwe.”

24 Davide anapita kutchire kukabisala.+ Pa tsiku lokhala mwezi, mfumu inakhala pamalo ake kuti idye chakudya.+ 25 Iyo inakhala pamalo ake a nthawi zonse, pampando umene unali kufupi ndi khoma. Yonatani anakhala moyang’anizana ndi mfumuyo, pamene Abineri+ anakhala pambali pa Sauli. Koma mpando wa Davide unali wopanda munthu. 26 Pa tsiku limeneli Sauli sananene chilichonse, pakuti mumtima mwake anaganiza kuti: “China chake chachitika, ayenera kuti wadetsedwa,+ ndipo sanayeretsedwe.” 27 Tsiku lotsatizana ndi tsiku lokhala mwezi, tsiku lachiwiri, mpando wa Davide unakhalabe wopanda munthu. Choncho Sauli anafunsa mwana wake Yonatani kuti: “N’chifukwa chiyani mwana wa Jese+ sanabwere ku chakudya dzulo ndi lero?” 28 Yonatani anayankha Sauli kuti: “Davide anandichonderera kuti ndimulole kuchoka kuti apite ku Betelehemu.+ 29 Anandiuza kuti, ‘Chonde ndilole ndipite kumzinda wakwathu kukapereka nsembe ya banja lathu. M’bale wanga ndi amene wandiitanitsa. Choncho ngati ungandikomere mtima, chonde ndilole ndichoke mwakachetechete ndiponso mofulumira kuti ndikaone abale anga.’ N’chifukwa chake sanabwere kudzadya chakudya pamodzi ndi mfumu.” 30 Ndiyeno Sauli anamukwiyira kwambiri+ Yonatani, ndipo anamuuza kuti: “Chimwana cha mkazi wopanduka iwe.+ Ukuganiza sindikudziwa kuti wasankha kugwirizana ndi mwana wa Jese, ndi kudzichititsa wekha manyazi ndiponso kuvula mayi ako?+ 31 Masiku onse amene mwana wa Jeseyo adzakhala ndi moyo, iweyo ndi ufumu wako sudzakhazikika ayi.+ Choncho tumiza anthu akamugwire ndi kumubweretsa kwa ine, pakuti ayenera kufa ndithu.”+

32 Koma Yonatani anayankha Sauli bambo ake kuti: “Aphedwe chifukwa chiyani?+ Walakwanji?”+ 33 Atatero, Sauli anaponya mkondo wake kuti amulase.+ Pamenepo Yonatani anadziwa kuti bambo ake anatsimikiza mtima kupha Davide.+ 34 Nthawi yomweyo, Yonatani ananyamuka patebulopo atakwiya kwambiri,+ ndipo sanadye mkate tsiku lachiwiri lotsatizana ndi tsiku lokhala mwezi. Iye anachita zimenezi chifukwa chopwetekedwa mtima ndi nkhani ya Davide,+ pakuti bambo ake anam’chititsa manyazi.+

35 M’mawa mwake, Yonatani pamodzi ndi mtumiki wake wachinyamata anapita kutchire kumene anapangana kukakumana ndi Davide.+ 36 Ndiyeno anauza mtumiki wakeyo kuti: “Chonde, thamanga kuti ukatole mivi imene ndikuponya.”+ Mtumikiyo anathamanga, ndipo Yonatani anaponya muvi kuti upitirire mtumikiyo. 37 Mtumiki uja atafika pamalo amene muvi wa Yonatani unagwera, Yonatani anayamba kumufuulira kumbuyo kwake kuti: “Kodi muvi sunagwere patali kwambiri ndi pamene iwe uli?”+ 38 Zitatero, Yonatani anapitiriza kufuulira mtumiki uja kuti: “Fulumira! Chita changu! Usaime!” Ndiyeno mtumiki wa Yonatani anatola miviyo ndi kubwera nayo kwa mbuye wake. 39 Koma mtumikiyo sanadziwe kalikonse. Yonatani ndi Davide okha ndi amene anali kudziwa zimene zinali kuchitika. 40 Kenako, Yonatani anapatsa mtumiki wakeyo zida zake ndi kumuuza kuti: “Tenga zidazi ndi kupita nazo kumzinda.”

41 Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+ 42 Pamenepo Yonatani anauza Davide kuti: “Pita mu mtendere,+ pakuti tonse awiri talumbira+ m’dzina la Yehova kuti, ‘Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.’”+

Chotero Davide ananyamuka ndi kupita, koma Yonatani anabwerera kumzinda.

21 Kenako Davide anafika ku Nobu+ kwa Ahimeleki wansembe. Ahimeleki+ ataona Davide anayamba kunjenjemera, ndipo anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani uli wekha popanda munthu wina?”+ 2 Pamenepo Davide anauza Ahimeleki wansembe kuti: “Mfumu yandituma nkhani inayake,+ ndipo yandiuza kuti, ‘Usauze munthu aliyense nkhani imene ndikukutuma ndi zimene ndakulamula.’ Choncho ndapangana ndi anyamata kuti ndikumane nawo pamalo enaake. 3 Ndiye ngati muli ndi mitanda isanu ya mkate kapena chilichonse chimene chingapezeke, ndipatseni.”+ 4 Koma wansembeyo anayankha Davide kuti: “Ndilibe mkate wamba, koma pali mkate wopatulika.+ Nditha kukupatsa umenewu ngati anyamatawo ayesetsa kudzisunga osagona ndi akazi.”+ 5 Davide anayankha wansembeyo kuti: “Koma akazi sanatiyandikire monga mmene zinakhaliranso poyamba pamene ndinapita kukamenya nkhondo.+ Anyamatawo amakhala oyera ngakhale pamene tili pa ntchito wamba. Ndiye kuli bwanji lero pamene tili pa ntchito yapadera?” 6 Pamenepo wansembeyo anam’patsa mkate wopatulika,+ chifukwa panalibe mkate wina koma mkate wachionetsero wokha, umene anali atauchotsa pamaso pa Yehova+ pa tsiku limenelo kuti aikepo watsopano.

7 Tsopano tsiku limenelo, mmodzi wa atumiki a Sauli, dzina lake Doegi,+ Mwedomu,+ anali kumeneko chifukwa anali atamusunga+ pamaso pa Yehova. Iye anali mkulu wa abusa a Sauli.+

8 Davide anafunsa Ahimeleki kuti: “Kodi muli ndi chida chilichonse pano, mkondo kapena lupanga? Inetu sindinatenge lupanga kapena zida zanga, pakuti zimene mfumu yandituma zinali kufunika mofulumira.” 9 Wansembeyo poyankha anati: “Lupanga la Goliyati+ Mfilisiti amene unamukantha m’chigwa cha Ela+ lilipo. Lakulungidwa ndi nsalu ndipo lili kuseli kwa efodi.+ Ngati ungakonde kutenga limeneli, litenge, chifukwa palibenso lupanga lina.” Pamenepo Davide anati: “Palibe lina lingafanane nalo, ndipatseni limenelo.”

10 Pamenepo Davide ananyamuka tsiku limenelo, ndipo anapitiriza kuthawa+ chifukwa choopa Sauli. Patapita nthawi anafika kwa Akisi mfumu ya Gati.+ 11 Atafika kumeneko, atumiki a Akisi anayamba kunena kuti: “Kodi ameneyu si Davide+ mfumu ya dziko? Suja ankamuimbira nyimbo molandizana mawu, akuvina+ n’kumati,

‘Sauli wakantha adani ake masauzande,

Ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi’?”+

12 Davide atamva zimenezi, anachita mantha kwambiri+ chifukwa cha Akisi mfumu ya Gati. 13 Chotero iye anadzibisa+ kuti asadziwike kuti ndi munthu wabwinobwino,+ moti pamene anali m’manja mwawo anayamba kuchita zinthu ngati munthu wamisala. Iye anayamba kulembalemba pazitseko za pachipata, dovu lili chuchuchu, likuyenderera pandevu zake. 14 Pamapeto pake Akisi anauza atumiki ake kuti: “Mukuona kuti munthuyu ndi wamisala. N’chifukwa chiyani mwabwera naye kwa ine? 15 Kodi ine ndikufuna anthu amisala, kuti mundibweretsere munthu ameneyu kudzachita zamisala pamaso panga? Kodi ameneyu ndi woyenera kulowa m’nyumba mwanga?”

22 Choncho Davide anachoka kumeneko+ ndi kuthawira+ kuphanga+ la Adulamu.+ Abale ake ndi nyumba yonse ya bambo ake anamva zimenezo, ndipo ananyamuka kumutsatira. 2 Amuna onse amene anali kusautsidwa,+ onse amene anali ndi ngongole,+ ndi onse amene anali ndi zodandaula+ anayamba kusonkhana kwa iye,+ ndipo iye anakhala mtsogoleri wawo.+ Anthu onse amene anali naye anakwana 400.

3 Kenako Davide anachoka kupita ku Mizipe, ku Mowabu ndi kupempha mfumu ya Mowabu+ kuti: “Chonde, lolani kuti bambo ndi mayi anga+ akhale nanu kufikira nditadziwa zimene Mulungu adzandichitira.” 4 Chotero iye anawasiya m’manja mwa mfumu ya Mowabu, moti iwo anapitiriza kukhala kumeneko masiku onse amene Davide anakhala m’malo ovuta kufikako.+

5 Patapita nthawi, Gadi+ mneneri anauza Davide kuti: “Usakhalenso m’malo ovuta kufikako. Uchokeko ndi kubwera m’dziko la Yuda.”+ Choncho Davide anachokako ndi kulowa munkhalango ya Hereti.

6 Ndiyeno Sauli anamva kuti Davide ndi anthu amene anali naye apezeka. Iye anamva zimenezi ali ku Gibeya pamalo okwezeka, atakhala pansi pa mtengo wa bwemba.+ Sauliyo anali atagwira mkondo+ m’manja mwake ndipo atumiki ake onse anali atamuzungulira. 7 Iye anauza atumiki ake amene anali atamuzungulirawo kuti: “Tamverani inu Abenjamini. Kodi nayenso mwana wa Jese+ adzakupatsani minda ya mpesa ndi minda ya mbewu zina?+ Kodi nonsenu adzakuikani kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 100? 8 Pakuti nonsenu mwandikonzera chiwembu chifukwa palibe aliyense amene anaulula kwa ine+ pamene mwana wanga anachita pangano+ ndi mwana wa Jese. Palibenso aliyense wa inu amene wandimvera chifundo ndi kuulula kwa ine kuti mwana wanga weniweni wasandutsa mtumiki wanga kukhala wondibisalira kuti andichite chiwembu monga mmene zililimu.”

9 Pamenepo Doegi,+ Mwedomu, amene anali mkulu wa atumiki a Sauli anayankha kuti: “Ineyo ndinaona mwana wa Jese atabwera ku Nobu kwa Ahimeleki,+ mwana wa Ahitubu.+ 10 Ndipo Ahimeleki anafunsira+ kwa Yehova m’malo mwa Davide, kenako anam’patsa chakudya+ ndi lupanga+ la Goliyati Mfilisiti.” 11 Nthawi yomweyo mfumu inatumiza anthu kuti akaitane Ahimeleki wansembe, mwana wa Ahitubu, pamodzi ndi nyumba yonse ya bambo ake, ansembe a ku Nobu.+ Choncho onsewo anabwera kwa mfumu.

12 Pamenepo Sauli anati: “Tamvera iwe mwana wa Ahitubu.” Ndipo Ahimeleki anayankha kuti: “Ndikumva mbuyanga.” 13 Ndiyeno Sauli anapitiriza kumuuza kuti: “N’chifukwa chiyani anthu inu mwandikonzera chiwembu,+ iweyo ndi mwana wa Jese? Iweyo wamupatsa mkate ndi lupanga, komanso wamufunsira kwa Mulungu kuti andiukire pondibisalira monga mmene zililimu.”+ 14 Ahimeleki anayankha mfumuyo kuti: “Ndani pakati pa atumiki anu onse ali ngati Davide,+ munthu wokhulupirika,+ mkamwini+ wa mfumu, mtsogoleri wa asilikali okulonderani ndiponso munthu wolemekezeka m’nyumba yanu?+ 15 Kodi ndayamba lero kumufunsira+ kwa Mulungu? Sindingachite zimene mukunenazo! Chonde, mfumu isaimbe mlandu ine mtumiki wanu ngakhalenso nyumba yonse ya bambo anga, pakuti ndinachita zonsezi mosadziwa chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu.”+

16 Koma mfumu inati: “Ufa ndithu+ Ahimeleki, pamodzi ndi nyumba yonse ya bambo ako.”+ 17 Pamenepo mfumu inauza asilikali othamanga+ amene anaima pamaso pake kuti: “Tembenukani ndi kupha ansembe a Yehova chifukwa ali kumbali ya Davide. Iwo anali kudziwanso kuti Davide ndi wothawa koma sanaulule kwa ine!”+ Koma atumiki a mfumuwo sanafune kutambasula manja awo kuti akanthe ansembe a Yehova.+ 18 Pamapeto pake mfumu inauza Doegi+ kuti: “Iwe, tembenuka ukanthe ansembewa!” Nthawi yomweyo Doegi, Mwedomu,+ anatembenuka n’kukantha ndi kupha+ ansembewo tsiku limenelo, amuna 85 ovala efodi+ wa nsalu. 19 Iye anakanthanso ndi lupanga Nobu,+ mzinda wa ansembe. Anapha amuna, akazi, ana aang’ono ndi ana oyamwa, komanso ng’ombe zamphongo, abulu ndi nkhosa.

20 Koma mwana mmodzi wamwamuna wa Ahimeleki, mwana wa Ahitubu, dzina lake Abiyatara+ anapulumuka n’kuthawa kutsatira Davide. 21 Ndiyeno Abiyatara anauza Davide kuti: “Sauli wapha ansembe a Yehova.” 22 Pamenepo Davide anauza Abiyatara kuti: “Tsiku lomwe lija ndinadziwa+ kuti mosalephera, Doegi, Mwedomu uja, akauza Sauli+ chifukwa Doegiyo anali kumeneko. Ineyo ndalakwira aliyense wa m’nyumba ya bambo ako. 23 Koma iwe khala ndi ine. Usachite mantha. Chifukwa aliyense amene akufunafuna moyo wanga akufunafunanso moyo wako, ndipo ndifunika kukuteteza.”+

23 Patapita nthawi, kunabwera anthu amene anauza Davide kuti: “Afilisiti akuthira nkhondo mzinda wa Keila,+ ndipo akufunkha zokolola zimene zili pamalo opunthira mbewu.”+ 2 Ndiyeno Davide anayamba kufunsira+ kwa Yehova, kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa?” Yehova anayankha Davide kuti: “Pita, ukamenyane ndi Afilisitiwo ndipo ukapulumutse Keila.” 3 Amuna amene anali kuyenda ndi Davide anamuyankha kuti: “Ngati tikuchita mantha tili mbali ino ya Yuda,+ ndiye kuli bwanji tikapita ku Keila kukamenyana ndi asilikali a Afilisiti!”+ 4 Choncho Davide anafunsiranso kwa Yehova.+ Tsopano Yehova anamuyankha kuti: “Nyamuka, pita ku Keila, chifukwa ndikupereka Afilisitiwo m’manja mwako.”+ 5 Chotero Davide anapita ku Keila ndi amuna amene anali kuyenda naye, kukamenyana ndi Afilisitiwo. Iye anawalanda ziweto zawo ndipo anapha Afilisiti ochuluka kwambiri, moti Davide anakhala mpulumutsi wa anthu a mumzinda wa Keila.+

6 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Abiyatara+ mwana wamwamuna wa Ahimeleki anathawira kwa Davide ku Keila, anapita kumeneko atatenga efodi+ m’manja mwake. 7 Patapita nthawi, Sauli analandira uthenga wonena kuti: “Davide ali ku Keila.”+ Pamenepo Sauli ananena kuti: “Mulungu wamugulitsa kwa ine,+ pakuti wadzitsekera yekha mwa kulowa mumzinda wokhala ndi zitseko ndi mipiringidzo.” 8 Choncho Sauli anaitanitsa anthu onse kuti apite ku Keila kukazungulira Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye, n’kuwathira nkhondo. 9 Davide anadziwa kuti Sauli akumukonzera chiwembu.+ Choncho anauza Abiyatara wansembe kuti: “Bweretsa efodi kuno.”+ 10 Atamupatsa, Davide anati: “Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ ine mtumiki wanu ndamva kuti Sauli akufuna kubwera kuno ku Keila kuti awononge mzindawu chifukwa cha ine.+ 11 Kodi anthu a mumzinda wa Keila adzandipereka m’manja mwake? Kodi Sauli abweradi kuno monga mmene ine mtumiki wanu ndamvera? Yehova Mulungu wa Isiraeli, ndiuzeni ine mtumiki wanu, chonde.” Pamenepo Yehova anamuyankha kuti: “Abweradi kuno.”+ 12 Ndiyeno Davide anafunsanso kuti: “Kodi anthu a mumzinda wa Keila adzandiperekadi m’manja mwa Sauli pamodzi ndi amuna amene ndikuyenda nawowa?” Poyankha, Yehova anati: “Adzaterodi.”+

13 Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi amuna pafupifupi 600+ amene anali kuyenda naye. Iwo anatuluka mu Keila ndi kumangoyendayenda kulikonse kumene akufuna. Ndiyeno uthenga unafika kwa Sauli kuti Davide wathawa ku Keila. Sauli atamva zimenezi sanapitekonso. 14 Tsopano Davide anayamba kukhala m’chipululu, m’malo ovuta kufikako. Iye anapitiriza kukhala m’dera lamapiri m’chipululu cha Zifi,+ ndipo Sauli anali kumufunafuna nthawi zonse,+ koma Mulungu sanam’pereke m’manja mwake.+ 15 Davide anapitiriza kukhala mwamantha chifukwa Sauli anali kufunafuna moyo wake, pamene Davideyo anali m’chipululu cha Zifi ku Horesi.*+

16 Tsopano Yonatani mwana wa Sauli ananyamuka ndi kupita kwa Davide ku Horesi, kuti akalimbikitse+ Davide kudalira Mulungu.+ 17 Ndiyeno anamuuza kuti: “Usachite mantha,+ chifukwa dzanja la Sauli bambo anga silikupeza, moti iwe ukhaladi mfumu+ ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe. Sauli bambo anga akudziwa bwino zimenezi.”+ 18 Kenako awiriwo anachita pangano+ pamaso pa Yehova. Zitatero, Davide anapitiriza kukhala ku Horesi koma Yonatani anabwerera kwawo.

19 Kenako amuna a ku Zifi+ anapita kwa Sauli ku Gibeya+ kukamuuza kuti: “Kodi Davide si uyu akubisala+ pafupi ndi ife m’malo ovuta kufikamo ku Horesi,+ paphiri la Hakila+ limene lili kudzanja lamanja* la Yesimoni?*+ 20 Choncho, malinga ndi chokhumba cha moyo wanu,+ mfumu, chofuna kubwera kuno, bwerani, ndipo ife tidzam’pereka m’manja mwa mfumu.”+ 21 Pamenepo Sauli anati: “Yehova akudalitseni,+ chifukwa mwandichitira chisoni. 22 Chonde pitani, mukayesetsebe kufufuza kwa aliyense amene anamuonayo, ndipo mukaone kumene iye amafika, pakuti ndauzidwa kuti ndi wochenjera kwambiri.+ 23 Mukaonetsetse ndi kutsimikizira za malo onse obisika kumene iye amabisala. Kenako mudzabwerenso kwa ine ndi umboni, ndipo ine ndidzapita nanu. Ngati alidi m’dzikolo, ndidzam’funafuna mosamala pakati pa anthu masauzande+ ambirimbiriwo a Yuda.”

24 Chotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi,+ Sauli atamusiya kumbuyo. Izi zinachitika pamene Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali m’chipululu cha Maoni,+ mu Araba,+ kum’mwera kwa Yesimoni. 25 Kenako Sauli anafika ndi asilikali ake kudzafunafuna Davide.+ Davide atauzidwa zimenezi, nthawi yomweyo analowa mkatikati mwa chipululu n’kukabisala kuthanthwe,+ ndipo anapitiriza kukhala m’chipululu cha Maoni. Sauli atamva zimenezo anayamba kuthamangitsa+ Davide m’chipululu chimenecho cha Maoni. 26 Kenako Sauli anakhala mbali imodzi ya phiri ndipo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali mbali inanso ya phirilo. Zitatero Davide ananyamuka mofulumira kuti athawe+ Sauli. Pa nthawiyi n’kuti Sauli ndi asilikali ake atatsala pang’ono kupeza ndi kugwira Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye.+ 27 Koma kunabwera mthenga kwa Sauli amene anamuuza kuti: “Bwererani mofulumira, Afilisiti aukira dziko!” 28 Pamenepo Sauli anasiya kum’thamangitsa Davide+ ndipo anabwerera kukakumana ndi Afilisiti. N’chifukwa chake malowo anawatcha Thanthwe Logawanitsa.

29 Ndiyeno Davide anachoka kumeneko ndi kukakhala m’malo ovuta kufikako a ku Eni-gedi.+

24 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Sauli atangobwerera kuchokera kothamangitsa Afilisiti,+ kunabwera uthenga wakuti: “Davide ali m’chipululu cha Eni-gedi.”+

2 Pamenepo Sauli anatenga amuna osankhidwa mwapadera 3,000+ mu Isiraeli monse, ndipo anapita kukafunafuna Davide+ ndi amuna amene anali kuyenda naye m’matanthwe amene mumakhala mbuzi za m’mapiri.+ 3 Patapita nthawi, Sauli anafika kumakola a nkhosa amiyala m’mphepete mwa msewu, kumene kunali phanga. Choncho Sauli analowa mmenemo kukadzithandiza.+ Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali atakhala pansi m’zigawo za mkatikati za phangalo,+ kumbuyo kwambiri. 4 Amuna amene anali ndi Davidewo anayamba kumuuza kuti: “Lerotu ndi tsiku limene Yehova akukuuzani kuti, ‘Taona, ndapereka mdani wako m’manja mwako,+ ndipo umuchitire chilichonse chimene ukuona kuti n’chabwino.’”+ Choncho Davide ananyamuka ndipo mwakachetechete anadula kansalu m’munsi mwa malaya akunja odula manja a Sauli. 5 Koma pambuyo pake, Davide anavutika mumtima mwake+ chifukwa chakuti anali atadula kansalu m’munsi mwa malaya akunja odula manja a Sauli. 6 Choncho iye anauza amuna amene anali kuyenda naye kuti: “Sindinayenere m’pang’ono pomwe kuchitira mbuyanga zimenezi pamaso pa Yehova. Iye ndi wodzozedwa+ wa Yehova. Sindinayenere kutambasula dzanja langa ndi kumuukira, pakuti iye ndi wodzozedwa wa Yehova.”+ 7 Chotero ndi mawu amenewa, Davide anabalalitsa amuna amene anali kuyenda naye, ndipo sanawalole kuti aukire Sauli.+ Koma Sauli ananyamuka ndi kutuluka m’phangamo.

8 Pambuyo pake, Davide nayenso anatuluka m’phangamo ndi kuitana Sauli kuti: “Mbuyanga+ mfumu!” Pamenepo Sauli anacheuka ndipo Davide anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 9 Ndiyeno Davide anauza Sauli kuti: “N’chifukwa chiyani mukumvera mawu a anthu,+ akuti, ‘Davide akufuna kukuvulazani’? 10 Lero mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani m’manja mwanga m’phangamu. Winawake anandiuza kuti ndikupheni,+ koma ndinakumverani chisoni n’kunena kuti, ‘Sindingatambasule dzanja langa ndi kuukira mbuyanga, pakuti iye ndi wodzozedwa+ wa Yehova.’ 11 Tsopano, bambo anga,+ onani. Taonani kansalu ka m’munsi mwa malaya anu akunja odula manja. Pakuti mmene ndinali kudula kansalu kameneka sindinakupheni. Ndiyetu dziwani ndi kuona kuti ndilibe maganizo oipa+ kapena oukira, ndipo sindinakuchimwireni, ngakhale kuti inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe.+ 12 Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu,+ ndipo Yehova andibwezerere,+ koma dzanja langali silidzakukhudzani.+ 13 Mwambi wa anthu akale umati, ‘Choipa chimachokera kwa munthu woipa,’+ koma dzanja langali silidzakukhudzani. 14 Kodi mfumu ya Isiraeli ikulondola ndani? Kodi mukuthamangitsa ndani? Zoona mukuthamangitsa galu wakufa?+ Nthata imodzi?+ 15 Yehova akhale woweruza, ndipo aweruze pakati pa ine ndi inu. Iye adzandiweruzira mlanduwu+ ndi kuchitapo kanthu kuti andimasule m’manja mwanu.”

16 Ndiyeno Davide atangomaliza kulankhula mawu amenewa kwa Sauli, Sauli anati: “Kodi ndi mawu ako, mwana wanga Davide?”+ Pamenepo Sauli anayamba kulira mokweza mawu.+ 17 Iye anapitiriza kuuza Davide kuti: “Ndiwe wolungama kwambiri kuposa ine,+ pakuti iwe wandichitira zabwino,+ koma ine ndakuchitira zoipa. 18 Lero iwe wasonyeza zabwino zimene wandichitira, pakuti Yehova anandipereka m’manja mwako+ koma iwe sunandiphe. 19 Tsopano ngati munthu wapeza mdani wake, kodi angamulole kupita mwamtendere?+ Chonchotu Yehova adzakufupa ndi zinthu zabwino,+ chifukwa chakuti lero wandichitira zabwino. 20 Taona! Ine ndikudziwa bwino kwambiri kuti mosalephera iweyo udzalamulira monga mfumu,+ ndipo ufumu wa Isiraeli udzakhazikika m’banja lako nthawi zonse. 21 Choncho ndilumbirire tsopano pali Yehova+ kuti sudzawononga mbewu yanga yobwera m’mbuyo mwanga, ndi kuti sudzafafaniza dzina langa m’nyumba ya bambo anga.”+ 22 Zitatero, Davide analumbirira Sauli. Kenako Sauliyo anapita kwawo,+ koma Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anapita kumalo ovuta kufikako.+

25 Patapita nthawi, Samueli+ anamwalira ndipo Aisiraeli onse anasonkhana pamodzi ndi kulira+ maliro ake. Iwo anamuika m’manda panyumba yake ku Rama.+ Kenako Davide ananyamuka ndi kupita kuchipululu cha Parana.+

2 Tsopano mwamuna wina anali kukhala ku Maoni,+ koma ntchito yake anali kugwirira ku Karimeli.*+ Mwamuna ameneyu anali wotchuka kwambiri, ndipo anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Tsiku lina, iye anali kugwira ntchito yometa ubweya+ wa nkhosa zake ku Karimeli. 3 Mwamuna ameneyu dzina lake anali Nabala,+ ndipo mkazi wake anali Abigayeli.+ Mkazi wakeyu anali wanzeru kwambiri+ ndi wokongola, koma mwamunayu anali wouma mtima ndi wokonda kuchita zinthu zoipa.+ Mwamuna ameneyu anali wa m’banja la Kalebe.+ 4 Davide ali kuchipululu, anamva kuti Nabala akumeta ubweya+ wa nkhosa zake. 5 Choncho Davide anatumiza anyamata ake 10 ndi kuwauza kuti: “Pitani ku Karimeli kwa Nabala mukam’funse za moyo wake m’dzina langa.+ 6 M’bale wangayo mukamuuze kuti, ‘Mtendere ukhale nawe+ pamodzi ndi onse a m’nyumba yako ndi zonse zimene uli nazo. 7 Ine ndamva kuti ukumeta ubweya wa nkhosa zako. Abusa ako anali ndi ife.+ Sitinawavutitse,+ ndipo masiku onse amene tinali nawo ku Karimeli, palibe kanthu kawo kamene kanasowa. 8 Funsa anyamata ako zimenezi ndipo akuuza. Motero uwakomere mtima anyamata anga chifukwa tabwera tsiku labwino. Chonde, ugawire atumiki ako ndi mwana wako Davide chilichonse chimene dzanja lako lingapeze.’”+

9 Chotero anyamata a Davide anapita kukauza Nabala mawu onsewa m’dzina la Davide ndi kuyembekezera. 10 Pamenepo Nabala anayankha atumiki a Davide kuti: “Kodi Davide ndani,+ ndipo mwana wa Jese ndani? Masiku ano atumiki amene akuthawa ambuye awo achuluka kwabasi.+ 11 Ndiye ine nditenge mkate wanga,+ madzi ndi nyama imene ndaphera anyamata anga ometa ubweya wa nkhosa n’kupereka kwa amuna amene sindikudziwa m’pang’ono pomwe kumene achokera?”+

12 Atamva zimenezi, anyamata a Davide anatembenuka ndi kubwerera, ndipo atafika anamuuza mawu onsewa. 13 Nthawi yomweyo, Davide anauza amuna amene anali kuyenda naye kuti: “Aliyense amange lupanga lake m’chiuno!”+ Pamenepo aliyense anamangadi lupanga lake m’chiuno, ndipo Davide nayenso anamanga lupanga lake m’chiuno. Zitatero, amuna pafupifupi 400 anapitira limodzi ndi Davide, koma amuna 200 anatsala kuti ayang’anire katundu.+

14 Izi zili choncho, mmodzi mwa anyamata a Nabala anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala kuti: “Davide anatumiza nthumwi zake kuchokera m’chipululu kudzafunira zabwino mbuyanga, koma mbuyanga walalatira+ nthumwizo. 15 Amuna amenewa anatichitira zabwino kwambiri, sanativutitse, moti masiku onse amene tinali kuyenda nawo kutchire sitinataye kanthu ngakhale kamodzi.+ 16 Iwo anali ngati khoma+ lotizungulira usana ndi usiku, masiku onse amene tinakhala nawo pamene tinali kuweta nkhosa. 17 Choncho mudziwe zimenezi ndi kuona zimene mungachite, chifukwa atsimikiza kudzetsa tsoka+ pa mbuyanga ndi onse a m’nyumba yake, pakuti mbuye wathu ndi munthu wopanda pake,+ sitingathe kulankhula naye.”

18 Nthawi yomweyo, Abigayeli+ anafulumira kutenga mitanda 200 ya mkate, mitsuko iwiri ikuluikulu ya vinyo,+ anapha nkhosa zisanu,+ anatenganso miyezo ya seya* isanu ya tirigu wokazinga,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100+ ndi nkhuyu zouma zoumba pamodzi 200+ ndi kuzikweza pa abulu. 19 Kenako anauza anyamata ake kuti: “Tsogolani,+ ine ndikubwera m’mbuyo mwanu.” Koma mwamuna wake Nabala sanamuuze kalikonse.

20 Ndiyeno pamene Abigayeli anali kutsika phiri atakwera bulu,+ mwadzidzidzi, anaona Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye akubwera, ndipo iye anakumana nawo. 21 Davide anali atanena kuti: “Ine ndinalondera zinthu zake m’chipululu ndipo palibe chinthu chake ngakhale chimodzi chimene chinasowa.+ N’zokhumudwitsa kuti munthu ameneyu akundibwezera zoipa pa zabwino zimene ndinam’chitira.+ 22 Choncho Mulungu alange mowirikiza+ adani a Davide, ngati ine ndidzasiya munthu aliyense wa m’nyumba ya Nabala wokodzera khoma*+ ali wamoyo kufikira m’mawa.”+

23 Abigayeli ataona Davide, nthawi yomweyo anatsika mofulumira pabulu wake. Iye anagwada pamaso pa Davide ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 24 Kenako anagwada pamapazi+ a Davide ndi kunena kuti: “Zolakwa zonse zikhale pa ine+ mbuyanga. Chonde, lolani kapolo wanu wamkazi alankhule nanu+ ndipo mvetserani mawu a kapolo wanu. 25 Chonde mbuyanga, musaganizire za Nabala, munthu wopanda pakeyu,+ chifukwa zochita zake ndi zogwirizana ndi dzina lake. Dzina lake ndi Nabala* ndipo ndi wopandadi nzeru.+ Koma ine kapolo wanu wamkazi sindinawaone anyamata amene inu mbuyanga munawatuma. 26 Tsopano mbuyanga, ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wanu:+ Yehova wakubwezani+ kuti musapalamule mlandu wamagazi+ komanso kuti musadzipulumutse nokha ndi dzanja lanu.+ Choncho lolani kuti adani anu ndi onse ofuna kukuvulazani mbuyanga, akhale ngati Nabala.+ 27 Ndiyeno mphatso*+ imene kapolo wanu wamkazi wabweretsa kwa inu mbuyanga, muipereke kwa anyamata amene akutsatira mapazi anu.+ 28 Chonde, khululukani kulakwa kwa kapolo wanu wamkazi,+ pakuti mosalephera Yehova adzakukhazikitsirani nyumba yachifumu, inu mbuyanga, ndipo idzakhalapo kwa nthawi yaitali,+ chifukwa inu mbuyanga mukumenya nkhondo za Yehova.+ Ndipo mwa inu simudzapezeka choipa chilichonse masiku onse a moyo wanu.+ 29 Munthu akakuukirani ndi kufunafuna moyo wanu, Yehova Mulungu+ adzakulunga ndi kuteteza moyo wanu m’phukusi la moyo+ monga mmene munthu amatetezera chuma chake. Koma moyo wa adani anu adzauponya ndi kuutaya kutali ngati mmene munthu amaponyera mwala ndi gulaye.*+ 30 Ndiye zimene zidzachitika n’zakuti, chifukwa chakuti Yehova adzachitira inu mbuyanga zabwino zimene wanena kwa inu, iye adzakuikani kukhala mtsogoleri wa Isiraeli.+ 31 Choncho musalole kuti zimenezi zikhale zokuvutitsani chikumbumtima ndi zokhumudwitsa mumtima mwanu mbuyanga, mwa kukhetsa magazi popanda chifukwa+ ndi kudzipulumutsa nokha ndi dzanja lanu.+ Mukatero, Yehova adzakuchitirani zabwino mbuyanga, ndipo mudzandikumbukire+ ine kapolo wanu wamkazi.”

32 Pamenepo Davide anauza Abigayeli kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene wakutumiza kudzakumana nane lero! 33 Iwenso udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako.+ Udalitsike chifukwa cha kundigwira lero kuti ndisapalamule mlandu wamagazi+ ndi kudzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.+ 34 Komabe, pali Yehova Mulungu wamoyo wa Isiraeli, amene wandigwira kuti ndisakuchitire choipa,+ ukanapanda kufulumira kudzakumana nane,+ ndithu sipakanatsala munthu wokodzera khoma+ m’banja la Nabala pofika mawa m’mawa.” 35 Atatero, Davide analandira zimene Abigayeli anamubweretsera ndiyeno anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwako mwamtendere.+ Taona, ndamvera mawu ako kuti ndichite zinthu mokuganizira.”+

36 Kenako Abigayeli anapita kwa Nabala ndipo anapeza kuti akuchita phwando m’nyumba mwake ngati phwando la mfumu.+ Nabala anali kusangalala kwambiri mumtima mwake ndipo anali ataledzereratu.+ Abigayeli sanamuuze chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu, kufikira m’mawa mwake. 37 Tsopano m’mawa mwake, vinyo atamuthera m’mutu, mkazi wake anayamba kumuuza zinthu zonsezi. Nabala atamva zimenezi, mtima wake+ unaferatu mkati mwake ndipo iye anakhala ngati mwala. 38 Patapita masiku 10, Yehova anakantha+ Nabala ndipo anafa.

39 Ndiyeno Davide anamva kuti Nabala wamwalira. Atatero, iye anati: “Adalitsike Yehova amene wandiweruzira mlandu+ ndi kundimasula ku chitonzo+ cha Nabala, komanso wagwira ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa.+ Yehova wabwezera zoipa za Nabala pamutu pake!”+ Pamenepo Davide anatumiza anthu kuti akamufunsirire Abigayeli, kuti akhale mkazi wake.+ 40 Choncho atumiki a Davide anapita ku Karimeli ndi kulankhula naye kuti: “Davide watituma kwa iwe kuti tikutenge ukakhale mkazi wake.” 41 Nthawi yomweyo, ananyamuka ndi kugwada mpaka nkhope yake pansi,+ n’kunena kuti: “Ine kapolo wanu ndine wokonzeka kukhala mtumiki wosambitsa mapazi+ a atumiki a mbuyanga.”+ 42 Kenako Abigayeli+ ananyamuka mofulumira ndi kukwera pabulu,+ atsikana ake asanu antchito akumutsatira pambuyo. Iye anatsatira nthumwi za Davide ndipo anakakhala mkazi wake.

43 Davide anali atatenganso Ahinowamu+ wa ku Yezereeli,+ ndipo onse awiriwa anakhala akazi ake.+

44 Koma Sauli anali atapereka Mikala+ mwana wake wamkazi, mkazi wake wa Davide, kwa Paliti,+ mwana wamwamuna wa Laisi wa ku Galimu.+

26 Patapita nthawi, amuna a ku Zifi+ anapita kwa Sauli ku Gibeya,+ ndipo anamuuza kuti: “Kodi simukudziwa kuti Davide akubisala kuphiri la Hakila+ moyang’anana ndi Yesimoni?”*+ 2 Pamenepo Sauli ananyamuka+ ndi kupita kuchipululu cha Zifi, pamodzi ndi amuna osankhidwa mwapadera 3,000+ a mu Isiraeli, kuti akafunefune Davide kuchipululuko. 3 Pamene Davide anali kukhala m’chipululu, Sauli anamanga msasa m’mphepete mwa msewu, paphiri la Hakila moyang’anana ndi Yesimoni. Ndiyeno Davide anamva kuti Sauli wabwera kudzam’sakasaka m’chipululumo. 4 Choncho Davide anatumiza azondi+ kuti akaone ngati Sauli wabweradi. 5 Pambuyo pake, Davide ananyamuka ndi kupita kumene Sauli anamanga msasa. Atafika kumeneko, Davide anaona pamene Sauli komanso Abineri+ mwana wa Nera, mtsogoleri wa gulu lankhondo, anagona. Sauli anali atagona mkati mwa mpanda wa msasa,+ ndipo anthu ena onse anagona momuzungulira. 6 Ndiyeno Davide anauza Ahimeleki Mhiti+ ndi Abisai+ mwana wa Zeruya,+ m’bale wake wa Yowabu, kuti: “Ndani atsike nane kupita kwa Sauli kumsasa?” Abisai anayankha kuti: “Ine ndipita nawe.”+ 7 Pamenepo Davide anapita kwa anthuwo usiku pamodzi ndi Abisai, ndipo atafika kumeneko anaona Sauli atagona mkati mwa mpanda wa msasawo, mkondo wake atauzika pansi chakumutu kwake. Ndipo Abineri ndi anthu ena onse anali atagona momuzungulira.

8 Tsopano Abisai anauza Davide kuti: “Lero Mulungu wapereka mdani wako m’manja mwako.+ Ndiye ndilole chonde, ndimubaye ndi kumukhomerera pansi ndi mkondo kamodzi kokha, sindichita kubwereza kawiri.” 9 Koma Davide anauza Abisai kuti: “Ayi, usamuphe. Kodi ndani anatambasula dzanja lake ndi kupha wodzozedwa wa Yehova,+ n’kukhala wopanda mlandu?”+ 10 Davide anapitiriza kunena kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ Yehova iye mwini adzamukantha,+ kapena tsiku lidzafika+ ndipo adzamwalira mmene amachitira wina aliyense, kapenanso adzapita kunkhondo+ ndipo adzaphedwa kumeneko.+ 11 Kwa ine, n’zosatheka!+ Sindingachite zimenezi pamaso pa Yehova.+ Sindingatambasule dzanja langa+ ndi kukantha wodzozedwa wa Yehova.+ Choncho, tiye titenge mkondo umene uli chakumutu kwakewo, ndi mtsuko wa madziwo tizipita.” 12 Chotero Davide anatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi zimene zinali chakumutu kwa Sauli n’kunyamuka. Palibe munthu anawaona+ kapena kuzindikira kalikonse kapenanso kudzuka, pakuti onse anali m’tulo. Tulo timene anagonato tinali tulo tofa nato,+ tochokera kwa Yehova. 13 Kenako Davide anapita kutsidya lina ndi kukaima pamwamba pa phiri, patali ndithu. Mtunda umene unali pakati pawo unali wautali kwambiri.

14 Tsopano Davide anayamba kuitana anthuwo ndi Abineri mwana wa Nera, kuti: “Kodi sukuyankha, Abineri?” Ndipo Abineri+ anayankha kuti: “Ndiwe ndani amene ukuitana mfumu?” 15 Pamenepo Davide anauza Abineri kuti: “Kodi iwe sindiwe mwamuna? Ndani angafanane nawe mu Isiraeli monse? Ndiye n’chifukwa chiyani sunayang’anire mbuye wako mfumu? Pakuti munthu wina anabwera kumeneko kuti adzaphe mbuye wako mfumu.+ 16 Zimene wachitazi si zabwino ayi. Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ anthu inu muyenera kufa ndithu,+ chifukwa simunayang’anire+ mbuye wanu. Ndithu simunayang’anire wodzozedwa wa Yehova.+ Tsopano taonani kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wake wa madzi+ zimene zinali chakumutu kwake.”

17 Pamenepo Sauli anazindikira mawu a Davide, ndipo anati: “Kodi ndi mawu ako, mwana wanga Davide?”+ Davide anayankha kuti: “Inde ndi mawu anga, mbuyanga mfumu.” 18 Davideyo anawonjezera kuti: “N’chifukwa chiyani inu mbuyanga mukuthamangitsa ine mtumiki wanu?+ Ndachita chiyani ine, ndipo ndalakwa chiyani?+ 19 Tsopano mbuyanga mfumu, mvetserani mawu a mtumiki wanu: Ngati Yehova ndiye wakutumani kuti mundiukire, iye alandire nsembe yanga yambewu.+ Koma ngati ndi ana a anthu,+ atembereredwe pamaso pa Yehova,+ chifukwa andipitikitsa ndi kundichotsa lero kuti ndisamve kuti ndili pafupi ndi cholowa cha Yehova,+ mwa kundiuza kuti, ‘Pita ukatumikire milungu ina!’+ 20 Tsopano musalole kuti magazi anga akhetsedwe pamaso pa Yehova,+ pakuti mfumu ya Isiraeli yapita kukasakasaka nthata imodzi,+ monga munthu wothamangitsa nkhwali imodzi m’mapiri.”+

21 Poyankha Sauli anati: “Ndachimwa.+ Bwerera mwana wanga Davide, pakuti sindidzakuvulaza chifukwa moyo wanga wakhala wamtengo wapatali+ kwa iwe lero. Taona, ndachita zinthu mopusa ndipo ndalakwitsa kwambiri.” 22 Ndiyeno Davide anayankha kuti: “Nawu mkondo wa mfumu, tumizani mmodzi mwa anyamata anu abwere kudzautenga. 23 Yehova adzabwezera aliyense malinga ndi chilungamo+ ndi kukhulupirika kwake, pakuti lero Yehova anakuperekani m’manja mwanga, koma sindinafune kutambasula dzanja langa ndi kukantha wodzozedwa wa Yehova.+ 24 Monga mmene lero moyo wanu wakhalira wamtengo wapatali kwa ine, moyo wanganso ukhale wamtengo wapatali pamaso pa Yehova+ kuti andipulumutse m’masautso anga onse.”+ 25 Pamenepo Sauli anauza Davide kuti: “Udalitsike mwana wanga Davide. Mosakayikira iwe udzachita ntchito zazikulu ndipo udzapambana ndithu.”+ Pamenepo Davide anachoka ndipo Sauli anabwerera kwawo.+

27 Koma Davide anati mumtima mwake: “Tsiku lina Sauli adzandipha ndithu. Palibe chimene ndingachite choposa kuthawira+ kudziko la Afilisiti.+ Ndiyeno Sauli adzagwa ulesi ndipo adzasiya kundifunafuna m’dziko lonse la Isiraeli.+ Pamenepo ndidzakhala nditapulumuka m’manja mwake.” 2 Choncho Davide pamodzi ndi amuna 600+ amene anali kuyenda naye ananyamuka ndi kupita kwa Akisi+ mfumu ya Gati, mwana wa Maoki. 3 Davide anapitiriza kukhala ndi Akisi ku Gati. Iye anakhala kumeneko pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye, ndipo aliyense mwa amunawo anali ndi banja lake.+ Davide anali ndi akazi ake awiri aja, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala. 4 Patapita nthawi, uthenga unafika kwa Sauli wonena kuti Davide anathawira ku Gati. Atamva zimenezo sanapitenso kukam’sakasaka.+

5 Kenako Davide anauza Akisi kuti: “Ngati mungandikomere mtima tsopano, lolani kuti andipatse malo mu umodzi mwa mizinda ing’onoing’ono kuti ndikakhale kumeneko. Nanga ine mtumiki wanu ndikhalirenji mumzinda wachifumu pamodzi ndi inu?” 6 Choncho Akisi anam’patsa mzinda wa Zikilaga+ pa tsiku limenelo. N’chifukwa chake mzinda wa Zikilaga wakhala wa mafumu a Yuda mpaka lero.

7 Choncho nthawi yonse imene Davide anakhala kumidzi ya Afilisiti inakwana chaka chimodzi ndi miyezi inayi.+ 8 Ndiyeno Davide pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye anapita kukathira nkhondo Agesuri,+ Agirezi ndi Aamaleki.+ Mitundu imeneyi inali kukhala m’dera loyambira ku Telami+ kukafika ku Shura,+ mpaka kukafika kudziko la Iguputo. 9 Davide anakantha dzikolo ndipo sanasiye mwamuna kapena mkazi aliyense ali wamoyo.+ Iye anatenga nkhosa, ng’ombe, abulu, ngamila ndi zovala. Atatero anabwerera ndi kupita kwa Akisi. 10 Ndiyeno Akisi anawafunsa kuti: “Kodi amunanu, lero munakamenya kuti nkhondo?” Poyankha, Davide anati:+ “Kum’mwera kwa dziko la Yuda,+ kum’mwera kwa dziko la Yerameeli+ ndi kum’mwera kwa Akeni.”+ 11 Davide sanasiye mwamuna ndi mkazi aliyense ali wamoyo kuti abwere nawo ku Gati, chifukwa ananena kuti: “Angakatinenere kuti, ‘Davide watichita zakutizakuti.’”+ (Izi n’zimene iye anali kuchita masiku onse amene anakhala kumidzi ya Afilisiti.) 12 Akisi anakhulupirira+ Davide, ndipo mumtima mwake anati: “Mosakayikira, Davide wakhala fungo lonunkha kwa anthu akwawo Aisiraeli,+ ndipo iye akhala mtumiki wanga mpaka kalekale.”

28 Ndiyeno masiku amenewo zinachitika kuti Afilisiti anayamba kusonkhanitsa asilikali awo kuti akamenyane ndi Isiraeli.+ Choncho, Akisi anauza Davide kuti: “Ndikukhulupirira kuti ukudziwa kuti iwe ndi anthu ako muyenera kupita ndi ine kunkhondo.”+ 2 Pamenepo Davide anauza Akisi kuti: “Ndiponso inu mukudziwa bwino zimene mtumiki wanu ayenera kuchita.” Chotero Akisi anauza Davide kuti: “Ndidzakuika kukhala msilikali wondilondera nthawi zonse.”+

3 Tsopano Samueli anali atamwalira ndipo Aisiraeli anali atamulira ndi kumuika m’manda mumzinda wakwawo ku Rama.+ Ndipo Sauli anali atachotsa anthu olankhula ndi mizimu ndi akatswiri olosera zam’tsogolo m’dzikolo.+

4 Ndiyeno Afilisiti anasonkhana pamodzi ndi kupita kukamanga msasa ku Sunemu.+ Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisiraeli onse pamodzi ndi kumanga msasa ku Giliboa.+ 5 Sauli ataona msasa wa Afilisiti anachita mantha kwambiri ndipo mtima wake unayamba kugunda.+ 6 Ngakhale kuti anali kufunsira kwa Yehova,+ Yehova sanamuyankhe+ kaya kudzera m’maloto,+ Urimu+ kapena kudzera mwa aneneri.+ 7 Pamapeto pake, Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndifufuzireni mkazi waluso polankhula ndi mizimu,+ ndipo ine ndipita kukalankhula naye.” Pamenepo atumiki ake anamuuza kuti: “Ku Eni-dori alipo mkazi waluso polankhula ndi mizimu.”+

8 Choncho Sauli anadzisintha+ ndi kuvala zovala zina. Atatero, iyeyo ndi amuna ena awiri anapita kwa mkaziyo ndipo anafikako usiku.+ Ndiyeno Sauliyo anati: “Ndiloserere zam’tsogolo+ mwa kulankhula ndi mizimu ndipo undiutsire munthu amene ndikuuze.” 9 Koma mkaziyo anauza Sauli kuti: “Iwe ukudziwa bwino zimene Sauli anachita. Ukudziwa kuti m’dziko lino anachotsamo anthu olankhula ndi mizimu ndiponso akatswiri olosera zam’tsogolo.+ Ndiye n’chifukwa chiyani ukufuna kunditchera msampha kuti ndiphedwe?”+ 10 Nthawi yomweyo, Sauli anamulumbirira m’dzina la Yehova kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ sukhala ndi mlandu chifukwa cha nkhani imeneyi!” 11 Pamenepo mkaziyo anati: “Ukufuna ndikuutsire ndani?” Poyankha Sauli anati: “Ndiutsire Samueli.”+ 12 Mkaziyo ataona “Samueli”*+ anayamba kulira mofuula kwambiri. Kenako mkaziyo anauza Sauli kuti: “N’chifukwa chiyani mwandipusitsa, pamene inuyo ndinu Sauli amene?” 13 Koma mfumu inamuuza kuti: “Usachite mantha. Waona chiyani?” Mkaziyo anayankha Sauli kuti: “Ndaona mulungu+ akutuluka m’nthaka.” 14 Nthawi yomweyo Sauli anafunsa mkaziyo kuti: “Akuoneka bwanji?” Ndipo mkaziyo anayankha kuti: “Amene watulukayu akuoneka kuti ndi mwamuna wokalamba ndipo wavala malaya akunja odula manja.”+ Atamva zimenezi, Sauli anazindikira kuti ameneyo ndi “Samueli”+ ndipo Sauliyo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi, kenako anagona pansi.

15 Pamenepo “Samueli” anafunsa Sauli kuti: “N’chifukwa chiyani wandisokoneza ndi kundidzutsa?”+ Sauli anayankha kuti: “Zinthu zandivuta kwambiri,+ pakuti Afilisiti akumenyana nane ndipo Mulungu wandichokera+ moti sakundiyankhanso, kaya kudzera mwa aneneri kapena m’maloto.+ N’chifukwa chake ndabwera kudzafunsa inu kuti mundiuze zimene ndiyenera kuchita.”+

16 Ndiyeno “Samueli” anamuyankha kuti: “Ndiye ukudzandifunsiranji pamene Yehova wakuchokera+ ndipo wakhala mdani wako?+ 17 Yehova achitadi zimene ananena kudzera mwa ine, ndipo Yehova ang’amba ufumuwu kuuchotsa kwa iwe+ ndi kuupereka kwa mnzako Davide.+ 18 Achita zimenezi chifukwa sunamvere mawu a Yehova,+ ndipo sunasonyeze mkwiyo wake woyaka moto umene anali nawo pa Amaleki.+ N’chifukwa chaketu lero Yehova achite zimenezi kwa iwe. 19 Yehova aperekanso Isiraeli pamodzi ndi iwe m’manja mwa Afilisiti,+ moti mawa iweyo+ ndi ana ako+ mukhala ndi ine. Komanso Yehova aperekadi asilikali a Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.”+

20 Sauli atamva zimenezi, anadzigwetsa mofulumira ndi kugona pansi mantha atamugwira kwambiri chifukwa cha mawu a “Samueli.” Komanso analefuka kwambiri chifukwa chakuti sanadye chakudya masana onse ndi usiku wonse. 21 Ndiyeno mkazi uja anapita pamene panali Sauli ndipo anaona kuti wathedwa nzeru kwambiri. Choncho anamuuza kuti: “Ineyo mtumiki wanu ndamvera mawu anu ndipo ndaika moyo wanga pangozi*+ pomvera mawu amene mwandiuza. 22 Tsopano inunso, chonde, mverani mawu a ine mtumiki wanu. Ndiloleni ndikupatseni mkate kuti mudye, mupezenso mphamvu chifukwa muli pa ulendo.” 23 Koma iye anakana ndipo anati: “Sindidya.” Atatero, atumiki ake pamodzi ndi mkaziyo anapitiriza kumulimbikitsa kuti adye. Pamapeto pake, anamvera mawu awo ndipo anadzuka pamene anagonapo n’kukakhala pampando. 24 Tsopano mkaziyo anali ndi mwana wa ng’ombe wonenepa+ m’nyumba yake. Choncho anam’pereka nsembe msangamsanga,+ ndipo anatenga ufa n’kuukanda ndi kuphika mikate yopanda chofufumitsa. 25 Kenako anapereka chakudyacho kwa Sauli ndi atumiki ake ndipo iwo anadya. Atamaliza ananyamuka usiku womwewo.+

29 Ndiyeno Afilisiti+ anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, pamene Aisiraeli anamanga msasa pafupi ndi kasupe amene anali ku Yezereeli.+ 2 Olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anali kudutsa m’magulu a asilikali 100, ndi 1,000, ndipo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anadutsa pambuyo pawo limodzi ndi Akisi.+ 3 Ndiyeno akalonga a Afilisiti anayamba kunena kuti: “Kodi Aheberi+ awa akufuna chiyani kuno?” Pamenepo Akisi anayankha akalonga a Afilisitiwo kuti: “Kodi uyu si Davide, mtumiki wa Sauli, mfumu ya Isiraeli? Iyetu wakhala ndi ine kuno kwa chaka chimodzi kapena ziwiri,+ ndipo kuyambira tsiku limene anathawira kwa ine kufikira lero, sindinam’peze+ ndi chifukwa ngakhale chimodzi.” 4 Pamenepo akalonga a Afilisiti anam’psera mtima kwambiri Akisi, ndipo anati: “Muuze abwerere,+ apite kumalo amene unam’patsa. Usamulole kuti apite nafe kunkhondo chifukwa angakatitembenukire+ kumeneko. Ukuganiza kuti munthu ameneyu adzakometsera dzina lake ndi chiyani kwa mbuye wake? Si mitu ya asilikali athu kodi? 5 Kodi uyu si Davide uja amene ankamuimbira nyimbo molandizana mawu, akuvina n’kumati, ‘Sauli wakantha adani ake masauzande, ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi’?”+

6 Choncho Akisi+ anaitana Davide ndi kumuuza kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ iweyo ndiwe wowongoka mtima, ndipo ndasangalala+ kuti wabwera nane+ kunkhondo, pakuti sindinapeze choipa chilichonse mwa iwe kuyambira tsiku limene unabwera kwa ine kufikira lero.+ Koma olamulira ogwirizana+ sakukuona bwino. 7 Choncho, bwerera mwamtendere, kuti usachite chilichonse chimene olamulira ogwirizana a Afilisiti angachione kukhala choipa.” 8 Koma Davide anayankha Akisi kuti: “Ndibwerere chifukwa chiyani? Ndalakwa chiyani,+ ndipo mwapeza chiyani mwa ine mtumiki wanu kuchokera pa tsiku limene ndinabwera kudzakhala nanu kufikira lero,+ kuti ndisapite kukamenyana ndi adani anu mbuyanga mfumu?” 9 Pamenepo Akisi anayankha Davide kuti: “Ndikudziwa bwino kuti wakhala ukundichitira zinthu zabwino, ngati mngelo wa Mulungu.+ Koma akalonga a Afilisiti ndi amene anena kuti, ‘Musalole kuti ameneyu apite nafe kunkhondo.’ 10 Choncho udzuke m’mawa kwambiri pamodzi ndi atumiki a mbuye wako amene anabwera nawe pamodzi. Mukangoona kuti kwayera mudzuke ndi kunyamuka.”+

11 Chotero Davide anadzuka m’mawa kwambiri+ pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye ndi kubwerera kudziko la Afilisiti m’mawa umenewo. Koma Afilisitiwo anapita ku Yezereeli.+

30 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Davide ndi asilikali ake anali kubwerera ku Zikilaga+ tsiku lachitatu, Aamaleki+ anaukira anthu a kum’mwera* ndi a mumzinda wa Zikilaga ndi kufunkha zinthu zawo. Iwo anathira nkhondo mzindawo ndi kuutentha ndi moto. 2 Aamalekiwo anatenga akazi+ a mumzindawo ndi zonse zimene zinali mmenemo. Sanaphe aliyense koma anawatenga ndi kupita nawo. 3 Davide atafika mumzindawo pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye, anangoona kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi agwidwa ndi kutengedwa. 4 Pamenepo Davide ndi anthu amene anali naye anayamba kulira mofuula+ mpaka kulefuka osathanso kulira. 5 Akazi awiri a Davide nawonso anali atatengedwa, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala. 6 Zimenezi zinam’vutitsa maganizo kwambiri Davide+ chifukwanso anthu anali kukambirana zom’ponya miyala.+ Anthuwo anali kukambirana zimenezi chifukwa aliyense wa iwo anali wokwiya kwambiri+ poona zimene zachitikira ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Choncho, Davide anadzilimbitsa mwa Yehova Mulungu wake.+

7 Zitatero, Davide anauza Abiyatara+ wansembe, mwana wa Ahimeleki kuti: “Chonde, bweretsa efodi+ kuno.” Pamenepo Abiyatara anapereka efodi kwa Davide. 8 Ndiyeno Davide anayamba kufunsira kwa Yehova,+ kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la achifwambali? Kodi ndiwapeza?” Pamenepo anamuyankha+ kuti: “Inde athamangitse chifukwa uwapezadi ndi kulanditsa zinthu zimene afunkha.”+

9 Mwamsanga, Davide ananyamuka pamodzi ndi amuna 600+ amene anali kuyenda naye. Iwo anayenda mpaka kukafika kuchigwa* cha Besori, ndipo amuna ena anatsala pamenepo. 10 Davide pamodzi ndi amuna 400 anapitiriza kuwathamangitsa,+ koma amuna 200 amene anatopa kwambiri ndipo sanathe kuwoloka chigwa cha Besori+ anaima pomwepo.

11 Ndiyeno anapeza mwamuna wina wa ku Iguputo+ patchire. Choncho anamutengera kwa Davide ndi kumupatsa mkate kuti adye ndi madzi kuti amwe. 12 Anamupatsanso chidutswa cha nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndi zidutswa ziwiri za mphesa zouma zoumba pamodzi.+ Iye anadya ndipo anapezanso mphamvu,+ chifukwa sanadye mkate kapena kumwa madzi kwa masiku atatu, usana ndi usiku. 13 Ndiyeno Davide anamufunsa kuti: “Uli mbali ya ndani, ndipo kwanu n’kuti?” Mwamunayo anayankha kuti: “Ndine Mwiguputo, kapolo wa Mwamaleki, koma mbuyanga anandisiya pano masiku atatu apitawa chifukwa cha kudwala.+ 14 Ndife amene tinakaukira kum’mwera kwa dziko la Akereti+ ndi dera la Yuda komanso kum’mwera kwa dera la Kalebe.+ Ndipo mzinda wa Zikilaga tinautentha ndi moto.” 15 Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Kodi ungandiperekeze kumene kuli gulu la achifwambali?” Poyankha, iye anati: “Ndilumbirire+ pamaso pa Mulungu kuti sundipha, komanso kuti sundipereka m’manja mwa mbuyanga.+ Ukatero ndikuperekeza kumene kuli gulu la achifwambali.”

16 Chotero mwamunayo anaperekeza+ Davide ndi kupita kumene kunali achifwambawo, ndipo anawapeza atamwazikana m’dziko lonselo, akudya ndi kumwa, kuchita chiphwando+ chifukwa chakuti anafunkha zinthu zambiri m’dziko la Afilisiti ndi la Yuda.+ 17 Ndiyeno Davide anawakantha ndi kuwawononga, kuyambira m’bandakucha kufikira madzulo. Palibe aliyense wa iwo amene anathawa,+ kupatulapo anyamata 400 amene anakwera ngamila n’kuthawa. 18 Davide analanditsa zonse zimene Aamaleki anatenga,+ n’kulanditsanso akazi ake awiri aja. 19 Palibe chinthu chawo chilichonse chimene chinasowa, ana aamuna kapena ana aakazi, ngakhalenso zinthu zimene anafunkha kwa iwo komanso chilichonse chimene anawatengera.+ Davide analanditsa zonsezo. 20 Choncho Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng’ombe zonse za Aamaleki komanso ziweto zonse zimene Aamaleki anawalanda. Kenako iwo anati: “Izi ndi zofunkha za Davide.”+

21 Patapita nthawi, Davide anafika kwa amuna 200+ amene anawasiya kuchigwa cha Besori, amene sanathe kupita ndi Davide pakuti anali otopa kwambiri. Pamenepo iwo ananyamuka kudzakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye. Davide atawayandikira, anawafunsa za moyo wawo. 22 Koma mwamuna aliyense woipa ndi wopanda pake+ mwa amuna onse amene anatsatira Davide anayamba kunena kuti: “Chifukwa chakuti amenewa sanapite nafe, sitiwapatsa zofunkha zimene talanditsazi. Koma aliyense tingomupatsa mkazi wake ndi ana ake basi, awatenge ndipo azipita.” 23 Koma Davide anati: “Ayi abale anga, musatero ndi zinthu zimene Yehova watipatsa.+ Iye watiteteza+ ndi kupereka m’manja mwathu gulu la achifwamba limene linadzatiukira.+ 24 Ndani angamve zimene mukunenazo? Pakuti gawo limene munthu amene anapita kunkhondo alandire, likhala lofanana ndi gawo limene munthu amene anali kulondera katundu alandire.+ Aliyense alandirapo kenakake.”+ 25 Ndiyeno kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo, limeneli linakhala lamulo ndi chigamulo+ kwa Aisiraeli kufikira lero.

26 Davide atafika ku Zikilaga anatumiza zina mwa zofunkhazo kwa mabwenzi ake,+ akulu a ku Yuda, n’kunena kuti: “Landirani mphatso*+ iyi kuchokera pa zimene tafunkha kwa adani a Yehova.” 27 Anatumiza zimenezi kwa akulu a ku Beteli,+ a ku Ramoti+ wakum’mwera, a ku Yatiri,+ 28 a ku Aroweli, a ku Sifimoti, a ku Esitemowa,+ 29 ndi a ku Rakala. Anatumizanso zimenezi kwa akulu okhala m’mizinda ya Ayerameeli+ ndi m’mizinda ya Akeni,+ 30 komanso kwa akulu a ku Horima,+ a ku Borasani,+ a ku Ataki, 31 a ku Heburoni+ ndi kumalo onse kumene Davide anafikako pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye.

31 Tsopano Afilisiti anali kumenyana ndi Isiraeli,+ ndipo amuna a Isiraeli anathawa pamaso pa Afilisiti, moti anali kuphedwa+ m’phiri la Giliboa.+ 2 Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo pamapeto pake anapha Yonatani,+ Abinadabu+ ndi Malikisuwa,+ ana aamuna a Sauli. 3 Nkhondo inam’kulira kwambiri Sauli, moti pamapeto pake oponya mivi ndi uta anamupeza ndipo anamuvulaza koopsa.+ 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundibaya komanso kundizunza.” Koma womunyamulira zida uja sanafune,+ chifukwa anali kuopa kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake ndi kuligwera.+ 5 Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa,+ nayenso anagwera palupanga lake ndipo anafera limodzi.+ 6 Chotero Sauli, ana ake atatu, ndi womunyamulira zida komanso asilikali ake onse, anafera limodzi pa tsiku limenelo.+ 7 Amuna a Isiraeli amene anali m’dera la m’chigwa ndiponso m’dera la Yorodano ataona kuti asilikali a Isiraeli athawa komanso kuti Sauli ndi ana ake afa, anayamba kuchoka m’mizinda yawo ndi kuthawa.+ Kenaka Afilisiti anabwera n’kuyamba kukhala m’mizindayo.+

8 Ndiyeno tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzavula zovala anthu ophedwa,+ anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa paphiri la Giliboa.+ 9 Iwo anadula mutu wa Sauli+ ndi kumuvula zida zake. Kenako anatumiza uthenga+ m’dziko lonse la Afilisiti, kunyumba za mafano awo+ ndi kwa anthu awo. 10 Pamapeto pake, anakaika zida zakezo+ m’nyumba ya zifaniziro za Asitoreti,+ ndipo anapachika mtembo wake pakhoma mumzinda wa Beti-sani.+ 11 Choncho, anthu okhala mumzinda wa Yabesi-giliyadi+ anamva zimene Afilisiti anamuchita Sauli. 12 Nthawi yomweyo, amuna olimba mtima ananyamuka ndi kuyenda usiku wonse kukachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pakhoma la ku Beti-sani. Kenako anabwerera ku Yabesi ndi kutentha mitemboyo kumeneko.+ 13 Atatero, anatenga mafupa awo+ ndi kuwaika m’manda+ pansi pa mtengo wa bwemba+ ku Yabesi. Pambuyo pake, anasala kudya masiku 7.+

Dzinali limatanthauza, “Dzina la Mulungu,” kapena kuti “kuitana pa dzina la Mulungu.”

Akutchedwa Mwefuraimu chifukwa anali kukhala kudera la Efuraimu, koma kwenikweni Elikana anali Mlevi. Onani 1Mb 6:19, 22-28.

Onani mawu a mmunsi pa Mutu wa buku lino.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.

Chiheberi, “kubwereketsa.”

Ameneyu ndi Elikana. Onani 1Sa 2:11.

Kawirikawiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “nyanga” monga chizindikiro cha nyonga, mphamvu kapena ulamuliro.

Mawu akuti “nyumba” akutanthauza mzere wa ansembe.

Dzinali limatanthauza, “Ulemerero Uli Kuti?”

Mawu akuti “mbali yooneka ngati nsomba,” mawu ake enieni ndi “Dagoni yekha,” pakuti zikuoneka kuti fano la Dagoni linali mbali ina munthu mbali ina nsomba.

Onani mawu a m’munsi pa De 28:27.

Ena amaganiza kuti mawu akuti “anthu 50,000” anachita kuwawonjezera pambuyo pake.

Dzinali limatanthauza, “Mwala wa Thandizo.” “Ebenezeri” uyu ndi wosiyana ndi amene ali pa 1Sa 4:1 ndi pa 1Sa 5:1.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Onani mawu a m’munsi pa 1Mb 29:29.

Kapena kuti “patsindwi.”

Mawu akuti “mabanja anu” anganenedwenso kuti, “magulu anu a anthu 1,000.”

Onani mawu a m’munsi pa Eks 14:24.

M’Malemba achiheberi mulibe nambala yake.

Mipukutu ina ya Septuagint ndiponso Syriac Peshitta imati panali magaleta ankhondo “atatu.”

“Pimu” ndi muyezo wakale wolemera pafupifupi magalamu 8 a siliva.

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.

Mawu akuti “ekala” pano akutanthauza malo amene ng’ombe ziwiri zingathe kulima tsiku limodzi.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Mawu ake achiheberi angatanthauzenso “m’matangadza” kapena “mokondwera.”

Mawu ake enieni, “mzimu woipa wochokera kwa Yehova unam’vutitsa.”

“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Choncho iye anali wamtali pafupifupi mamita atatu.

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti “mphumphu 10 za tchizi.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala ndi dzanja chimene amachita kupukusa. M’madera ena amati mvuluma kapena ulaya.

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Mawu ake enieni, “anaika moyo wake m’dzanja lake.”

Kapena kuti, “atavala zovala zamkati zokha.”

Dzinali limatanthauza “Malo a Mitengo.”

Mawu akuti “kudzanja lamanja” ayenera kuti akunena kum’mwera kwa Yesimoni. Yerekezerani ndi vesi 24.

Kapena kuti “chipululu.”

Umenewu unali mzinda wa m’dera lamapiri la Yuda, umene unali pamtunda wa makilomita 12 kum’mwera kwa Heburoni. Si wofanana ndi phiri la Karimeli. Onani Yos 15:20, 54, 55.

Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita pafupifupi 8.

Mawuwa ndi mkuluwiko wachiheberi wotanthauza mwamuna.

Kutanthauza, “Wopanda Nzeru.”

Kapena kuti “dalitso.”

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 17:40.

Kapena kuti “chipululu.”

Nkhaniyi ikutchula zinthu malinga ndi mmene mkazi wolankhula ndi mizimu uja anali kuonera. Iye ananyengedwa ndi chiwanda chimene chinadziyerekezera kukhala Samueli.

Mawu ake enieni, “ndaika moyo wanga m’dzanja langa.”

Kumeneku ndi kum’mwera kwa Yuda.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Kapena kuti “dalitso.”

Ena amati “kugwaza.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena