Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Judges 1:1-21:25
  • Oweruza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Oweruza
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Oweruza

Oweruza

1 Ndiyeno zinachitika kuti Yoswa atamwalira,+ ana a Isiraeli anafunsira+ kwa Yehova kuti: “Ndani wa ife adzayamba kupita kwa Akanani kukamenyana nawo?” 2 Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Fuko la Yuda ndilo lidzayamba kupita.+ Ndipo ndidzaperekadi dzikolo m’manja mwawo.” 3 Ndiyeno a fuko la Yuda anauza abale awo a fuko la Simiyoni kuti: “Tiyeni tipitire limodzi m’gawo la fuko lathu+ kuti tikamenyane ndi Akanani. Kenako ifenso tidzapita nanu kugawo lanu.”+ Choncho fuko la Simiyoni linapita nawo.+

4 Pamenepo fuko la Yuda linakwezeka mtunda, ndipo Yehova anapereka Akanani ndi Aperezi m’manja mwawo,+ mwakuti anagonjetsa amuna 10,000 ku Bezeki. 5 Atapeza Adoni-bezeki ku Bezeki anamenyana naye mpaka kugonjetsa Akanani+ ndi Aperezi.+ 6 Pamenepo Adoni-bezeki anathawa, ndipo anam’thamangitsa ndi kum’gwira. Atam’gwira, anam’dula zala zamanthu za m’manja ndi zala zazikulu za kumapazi. 7 Zitatero, Adoni-bezeki anati: “Panali mafumu 70 odulidwa zala zamanthu za m’manja ndi zala zazikulu za kumapazi, amene anali kutola chakudya pansi pa tebulo langa. Mulungu wandibwezera zimene ndinachita.”+ Kenako anam’tengera ku Yerusalemu+ kumene anakafera.

8 Ndiyeno ana a Yuda anapitiriza kumenyana ndi mzinda wa Yerusalemu+ n’kuulanda. Anapha anthu okhala mmenemo ndi lupanga, ndipo mzindawo anautentha ndi moto. 9 Kenako ana a Yuda anatsika kukamenyana ndi Akanani okhala m’dera lamapiri, ku Negebu+ ndi ku Sefela.+ 10 Motero fuko la Yuda linapita kukamenyana ndi Akanani amene anali kukhala ku Heburoni,+ (poyamba dzina la mzinda wa Heburoni linali Kiriyati-ariba).+ Iwo anapha Sesai, Ahimani ndi Talimai.+

11 Atachoka kumeneko anapita kukamenyana ndi anthu a mumzinda wa Debiri.+ (Poyamba dzina la mzinda wa Debiri linali Kiriyati-seferi.)+ 12 Pamenepo Kalebe+ anati: “Ndithudi, aliyense amene amenyane ndi mzinda wa Kiriyati-seferi ndi kuulanda, ndim’patsa Akisa+ mwana wanga kuti akhale mkazi wake.”+ 13 Ndipo Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ mng’ono wake wa Kalebe, analanda mzindawo.+ Choncho, Kalebe anam’patsa Akisa mwana wake kuti akhale mkazi wake.+ 14 Ndiyeno zinachitika kuti pamene Akisa anali kupita kunyumba, anali kulimbikitsa Otiniyeli kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo ake. Kenako Akisa anawomba m’manja ali pabulu.*+ Atatero, Kalebe anamufunsa kuti: “Ukufuna chiyani?” 15 Ndipo iye anati: “Ndidalitseni,+ pakuti mwandipatsa malo akum’mwera, ndipo mundipatse Guloti-maimu.”* Pamenepo Kalebe anam’patsa Guloti Wakumtunda+ ndi Guloti Wakumunsi.

16 Ndiyeno ana a munthu wa mtundu wachikeni,+ amene anali apongozi ake a Mose,+ anatuluka mumzinda wa mitengo ya kanjedza+ pamodzi ndi ana a Yuda kukalowa m’chipululu cha Yuda, chimene chili kum’mwera kwa Aradi.+ Motero iwo anayamba kukhala pamodzi ndi anthuwo.+ 17 Koma a fuko la Yuda anayendabe ndi abale awo a fuko la Simiyoni, ndipo anapha Akanani okhala ku Zefati ndi kuwononga mzindawo.+ N’chifukwa chake mzindawo unatchedwa Horima.*+ 18 Kenako fuko la Yuda linalanda Gaza+ ndi madera ake, Asikeloni+ ndi madera ake ndiponso Ekironi+ ndi madera ake. 19 Yehova anakhalabe ndi fuko la Yuda, moti linalanda dera lamapiri, koma silinathe kupitikitsa anthu okhala m’chigwa, chifukwa chakuti anthuwo anali ndi magaleta*+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo.+ 20 Atapereka Heburoni kwa Kalebe monga mmene Mose analonjezera,+ Kalebe anapitikitsa ana atatu aamuna a Anaki amene anali kukhala mmenemo.+

21 Ana a Benjamini sanapitikitse Ayebusi amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ moti Ayebusiwo akukhalabe ndi ana a Benjamini m’Yerusalemu kufikira lero.+

22 Pa nthawi imeneyi, nawonso a nyumba ya Yosefe+ anapita kukamenyana ndi mzinda wa Beteli,+ ndipo Yehova anali nawo.+ 23 Pamenepo a nyumba ya Yosefe anayamba kuchita ukazitape+ pamzinda wa Beteli (poyamba dzina la mzindawu linali Luzi).+ 24 Ndiyeno azondi anaona mwamuna wina akutuluka mumzindawo, ndipo anamuuza kuti: “Tiuze mmene tingalowere mumzinda, ndipo tikukomera mtima.”+ 25 Iye anawauzadi mmene angalowere mumzindawo, ndipo iwo anapha anthu a mumzindawo ndi lupanga,+ koma anasiya mwamunayo ndi banja lake lonse ali amoyo.+ 26 Zitatero mwamunayo anapita kudziko la Ahiti+ ndi kumanga mzinda, n’kuutcha dzina lakuti Luzi. Limenelo ndilo dzina la mzindawo kufikira lero.

27 Manase+ sanatenge mzinda wa Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira, ndipo sanapitikitse anthu okhala mumzinda wa Dori+ ndi midzi yake yozungulira, anthu a mumzinda wa Ibuleamu+ ndi midzi yake yozungulira, ndi anthu okhala mumzinda wa Megido+ ndi midzi yake yozungulira. Akananiwo anakakamirabe kukhala m’dziko limeneli.+ 28 Ndiyeno zinachitika kuti Aisiraeli anakhala amphamvu,+ ndipo anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo,+ koma sanawachotseretu onse m’dzikolo.+

29 Fuko la Efuraimu nalonso silinapitikitse Akanani amene anali kukhala ku Gezeri, moti Akananiwo anakhalabe pakati pawo ku Gezeriko.+

30 Fuko la Zebuloni+ silinapitikitse anthu okhala mumzinda wa Kitironi ndi mzinda wa Nahaloli,+ moti Akananiwo anakhalabe pakati pawo+ ndipo a fuko la Zebuloni anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo.+

31 Fuko la Aseri+ silinapitikitse anthu okhala mumzinda wa Ako ndi anthu okhala m’mizinda ya Sidoni,+ Alabu, Akizibu,+ Heliba, Afiki+ ndi Rehobu.+ 32 Choncho Aaseri anapitirizabe kukhala pakati pa Akanani amene anali kukhala m’dzikolo, chifukwa chakuti sanawapitikitse.+

33 Fuko la Nafitali+ silinapitikitse anthu okhala m’mizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati,+ koma iwo anapitiriza kukhala pakati pa Akanani amene anali kukhala m’dzikolo.+ Ndipo fuko la Nafitali linayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo anthu okhala m’mizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati.+

34 Pamenepo Aamori anapitirizabe kupanikizira ana a Dani+ kudera lamapiri, ndipo sanawalole kutsikira m’chigwa.+ 35 Choncho Aamori anakakamirabe kukhala m’phiri la Herese ndi m’mizinda ya Aijaloni+ ndi Saalibimu.+ Koma dzanja la nyumba ya Yosefe linakhala lamphamvu kwambiri, moti anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Aamoriwo.+ 36 Dera la Aamori linali kuyambira kuchitunda cha Akirabimu,+ komanso ku Sela kupita chakumtunda.

2 Ndiyeno mngelo wa Yehova+ ananyamuka ku Giligala+ kupita ku Bokimu,+ ndipo anati: “Ndinakutulutsani mu Iguputo ndi kukulowetsani m’dziko limene ndinalumbirira makolo anu.+ Komanso ndinakuuzani kuti, ‘Sindidzaphwanya konse pangano langa ndi inu.+ 2 Ndipo inu musachite pangano ndi anthu okhala m’dziko ili,+ m’malomwake mugwetse maguwa awo ansembe.’+ Koma inu simunamvere mawu anga.+ N’chifukwa chiyani mwachita zimenezi?+ 3 Choncho nanenso ndikuti, ‘Sindiwapitikitsa pamaso panu, koma akhala msampha kwa inu,+ ndipo milungu yawo ikhala ngati nyambo.’”+

4 Mngelo wa Yehova atalankhula mawu amenewa kwa ana onse a Isiraeli, anthuwo anayamba kulira mokweza mawu.+ 5 Choncho anatcha malowo dzina lakuti Bokimu.* Ndipo anapereka nsembe kwa Yehova pamalowo.

6 Yoswa atauza anthuwo kuti apite, aliyense wa ana a Isiraeliwo anapita ku cholowa chake, kukatenga dzikolo kukhala lawo.+ 7 Ndipo anthuwo anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse a Yoswa ndi masiku onse a akulu amene anapitiriza kukhala ndi moyo Yoswa atamwalira, akulu amene anaona ntchito zonse zazikulu zimene Yehova anachitira Isiraeli.+ 8 Yoswa mtumiki wa Yehova, mwana wa Nuni, anamwalira ali ndi zaka 110.+ 9 Ndipo anamuika m’manda ku Timinati-heresi,*+ m’dera limene analandira monga cholowa chake, m’dera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.+ 10 Anthu onse a m’badwo umenewo anamwalira ndi kugona ndi makolo awo,+ ndipo pambuyo pawo panauka m’badwo wina umene sunadziwe Yehova kapena ntchito zimene iye anachitira Isiraeli.+

11 Ndiyeno ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova,+ n’kuyamba kutumikira Abaala.+ 12 Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ n’kuyamba kutsatira milungu ina mwa milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milungu imeneyo, moti anakhumudwitsa Yehova.+ 13 Anasiya Yehova ndi kuyamba kutumikira Baala ndi zifaniziro za Asitoreti.+ 14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Isiraeli,+ moti anawapereka m’manja mwa ofunkha, ndipo anayamba kufunkha zinthu zawo.+ Iye anawagulitsa kwa adani awo owazungulira+ moti sanathe kuima pamaso pa adani awo.+ 15 Kulikonse kumene apita, dzanja la Yehova linali kuwaukira ndi kuwadzetsera masoka,+ monga mmene Yehova ananenera ndiponso monga mmene Yehova analumbirira kwa iwo,+ moti iwo anali kuvutika kwambiri.+ 16 Zikatero, Yehova anali kuwapatsa oweruza,+ ndipo anali kuwapulumutsa m’manja mwa ofunkha.+

17 Ana a Isiraeli sanamvere ngakhale oweruza awo, koma anachita chiwerewere+ ndi milungu ina+ ndi kuigwadira. Iwo anapatuka mwamsanga panjira imene makolo awo anayendamo. Makolo awo anayenda m’njira imeneyo mwa kumvera malamulo a Yehova,+ koma iwo sanachite mofanana ndi makolo awo. 18 Yehova akawapatsa oweruza,+ Yehova anali kukhaladi ndi aliyense wa oweruzawo, ndipo iye anali kuwapulumutsa m’manja mwa adani awo masiku onse a moyo wa woweruzayo. Yehova anali kuchita zimenezo pakuti anali kuwamvera chisoni+ akamva kubuula kwawo chifukwa cha owapondereza ndi owakankhakankha.+

19 Ndiyeno zinali kuchitika kuti woweruza akamwalira, ana a Isiraeli anali kupatuka ndi kuchita zinthu zowawonongetsa kuposanso makolo awo. Anali kuchita zimenezi mwa kutsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Iwo sanasiye zochita zawozo ndiponso khalidwe lawo la unkhutukumve.+ 20 Chotero mkwiyo wa Yehova unayakira+ Isiraeli ndipo anati: “Popeza mtundu umenewu waphwanya pangano langa+ limene ndinalamula makolo awo kuti alisunge, ndipo sanamvere mawu anga,+ 21 ine sindipitikitsanso pamaso pawo mtundu uliwonse pa mitundu imene Yoswa anaisiya pamene ankamwalira.+ 22 Ndichita zimenezi kuti ndiyese+ Isiraeli kudzera mwa mitundu imeneyi, kuti ndione ngati angasunge njira ya Yehova mwa kuyendamo monga mmene makolo awo anachitira, kapena ayi.” 23 Choncho, Yehova analola mitundu imeneyi kukhalabe, osaipitikitsa mwamsanga,+ ndipo sanaipereke m’manja mwa Yoswa.

3 Pali mitundu+ imene Yehova anailola kukhalabe m’dzikoli n’cholinga choti ayese+ nayo Aisiraeli, kutanthauza Aisiraeli onse amene sanaonepo iliyonse mwa nkhondo zimene mtunduwo unamenya m’dziko la Kanani.+ 2 (Mitunduyo anailola kukhalabe kuti mibadwo ya ana a Isiraeli imene sinaonepo nkhondo, iphunzire ndi kudziwa kumenya nkhondo). 3 Mitunduyo ndi olamulira asanu ogwirizana+ a Afilisiti,+ Akanani onse,+ ngakhalenso Asidoni+ ndi Ahivi+ okhala m’phiri la Lebanoni,+ kuchokera kuphiri la Baala-herimoni+ mpaka kumalire a dera la Hamati.+ 4 Mulungu anapitirizabe kugwiritsa ntchito mitunduyo poyesa+ Aisiraeli, kuti aone ngati Aisiraeliwo adzamvera malamulo a Yehova amene anaperekedwa kwa makolo awo kudzera mwa Mose.+ 5 Ana a Isiraeli anakhala pakati pa Akanani,+ amene ndi Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 6 Aisiraeli anatenga ana aakazi a Akanani kukhala akazi awo,+ ndipo ana awo aakazi anawapereka kwa ana aamuna a Akanani,+ moti Aisiraeli anayamba kutumikira milungu ya Akanani.+

7 Chotero ana a Isiraeli anachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anaiwala Yehova Mulungu wawo,+ moti anayamba kutumikira Abaala+ ndi mizati yopatulika.+ 8 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Aisiraeli,+ moti anawagulitsa+ kwa Kusani-risataimu, mfumu ya Mesopotamiya.+ Ana a Isiraeli anatumikira Kusani-risataimu zaka 8. 9 Ndipo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Pamenepo Yehova anapereka mpulumutsi+ wa ana a Isiraeli kuti awapulumutse. Ameneyu anali Otiniyeli,+ mwana wamwamuna wa Kenazi,+ mng’ono wake wa Kalebe.+ 10 Mzimu+ wa Yehova unakhala pa iye, ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Siriya m’manja mwake, moti anam’gonjetsa.+ 11 Zitatero dziko linakhala pa mtendere zaka 40. Kenako Otiniyeli, mwana wa Kenazi, anamwalira.

12 Ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Pamenepo Yehova analola Egiloni mfumu ya Mowabu+ kukula mphamvu ndi kupondereza Isiraeli,+ chifukwa Aisiraeliwo anachita zoipa pamaso pa Yehova.+ 13 Kuwonjezera apo, anasonkhanitsa ana a Amoni+ ndi Amaleki+ kuti alimbane ndi Aisiraeli. Amenewa anakantha Isiraeli ndi kulanda mzinda wa mitengo ya kanjedza.+ 14 Ndipo ana a Isiraeli anatumikira Egiloni, mfumu ya Mowabu zaka 18.+ 15 Pamenepo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Choncho Yehova anawapatsa mpulumutsi, Ehudi,+ munthu wogwiritsa ntchito dzanja lamanzere,+ wa fuko la Benjamini,+ mwana wa Gera. M’kupita kwa nthawi, ana a Isiraeli anatumiza msonkho wawo kwa Egiloni mfumu ya Mowabu, kudzera mwa Ehudi. 16 Ehudi anali atadzipangira lupanga lakuthwa konsekonse,+ kutalika kwake mkono umodzi,* ndipo analimangirira m’chiuno kudzanja lamanja, mkati mwa chovala chake.+ 17 Atafika kwa Egiloni mfumu ya Mowabu,+ anapereka msonkho umene anabweretsa. Komatu Egiloni anali munthu wonenepa kwambiri.

18 Ehudi atapereka msonkhowo,+ anauza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. 19 Atafika pamiyala yogoba* imene inali ku Giligala,+ anabwerera kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “Pepanitu mfumu, ndili ndi uthenga wachinsinsi woti ndikuuzeni.” Pamenepo mfumuyo inati: “Khala chete!” Itatero, onse amene anaimirira pafupi ndi mfumuyo anatuluka.+ 20 Ehudi anafika kwa mfumuyo ili yokhayokha m’chipinda chapadera chozizira bwino, chimene chinali padenga.* Pamenepo Ehudi anati: “Uthenga umene ndili nawo ndi wochokera kwa Mulungu.” Atatero, mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu. 21 Pamenepo, Ehudi analowetsa dzanja lake lamanzere m’chovala chake, ndipo anasolola lupanga limene linali m’chiuno kudzanja lake lamanja ndi kulizika m’mimba mwa Egiloni. 22 Lupangalo linalowa ndi chigwiriro chomwe moti mafuta anaphimba lupangalo chifukwa sanalizule m’mimba mwakemo, ndipo chimbudzi chinayamba kutuluka. 23 Zitatero Ehudi anatulukira polowera mphepo, koma anasiya atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda cha padenga, 24 iyeyo n’kutuluka panja.+

Pamenepo atumiki a Egiloni anafika n’kuyamba kuyang’ana, ndipo anapeza zitseko za chipinda cha padenga zili zokhoma. Ndiyeno anati: “Ayenera kuti akudzithandiza+ m’chipinda chozizira bwino cha mkatikati.” 25 Iwo anapitiriza kudikira mpaka anataya mtima chifukwa anaona kuti mfumu sikutsegula zitseko za chipinda cha padenga. Pamenepo anatenga kiyi ndi kutsegula zitsekozo. Atatero anangoona mbuye wawo ali thasa pansi, wakufa.

26 Iwo akuganizaganiza zimene zachitika, Ehudi anathawa, ndipo anadutsa pamiyala yogoba+ ndi kuthawira ku Seira. 27 Atafika kumeneko anayamba kuliza lipenga la nyanga+ ya nkhosa m’dera lamapiri la Efuraimu.+ Iye ali patsogolo, ana a Isiraeli anatsika naye limodzi kuchoka m’dera lamapirilo. 28 Pamenepo anawauza kuti: “Nditsatireni,+ chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu, m’manja mwanu.”+ Atatero, anam’tsatira kukatsekereza Amowabu pamalo owolokera mtsinje+ wa Yorodano, ndipo sanalole aliyense kuwoloka. 29 Pa nthawi imeneyo anakantha amuna achimowabu 10,000.+ Aliyense mwa amunawo anali wojintcha+ ndipo aliyense wa iwo anali mwamuna wolimba mtima, koma palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+ 30 Chotero Mowabu anagonjetsedwa tsiku limenelo ndi Isiraeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere zaka 80.+

31 Pambuyo pa Ehudi panadzakhala Samagara+ mwana wamwamuna wa Anati. Ameneyu anapha amuna achifilisiti+ 600 ndi chisonga chotosera ng’ombe pozitsogolera. Ameneyunso anapulumutsa Isiraeli.+

4 Ehudi atamwalira, ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 2 Choncho Yehova anawagulitsa+ kwa Yabini mfumu yachikanani, imene inali kulamulira ku Hazori.+ Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera,+ yemwe anali kukhala ku Haroseti-ha-goimu.+ 3 Ana a Isiraeli anayamba kulirira Yehova,+ chifukwa Yabini anawapondereza+ kwambiri zaka 20, ndipo iye anali ndi magaleta ankhondo 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo.+

4 Pa nthawi imeneyo Debora mneneri wamkazi,+ mkazi wa Lapidoti, anali kuweruza Isiraeli. 5 Iye anali kukhala patsinde pa mtengo wa kanjedza wa Debora, pakati pa mzinda wa Rama+ ndi wa Beteli,+ m’dera lamapiri la Efuraimu. Ana a Isiraeli anali kupita kwa iye kukalandira zigamulo zochokera kwa Mulungu. 6 Ndiyeno iye anatumiza uthenga kwa Baraki+ mwana wa Abinowamu, yemwe anali ku Kedesi-nafitali,+ womuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli walamula kuti, ‘Tenga amuna 10,000 pakati pa ana a Nafitali+ ndi ana a Zebuloni+ ndipo mukasonkhane paphiri la Tabori.+ 7 Ine ndidzakokera kwa iwe+ m’chigwa* cha Kisoni,+ Sisera+ mkulu wa gulu lankhondo la Yabini,+ pamodzi ndi magaleta ake ankhondo ndi gulu lake lonse. Pamenepo ndidzam’pereka m’manja mwako.’”+

8 Ndiyeno Baraki anauza Debora kuti: “Ngati ungatsagane nane, ndipitadi, koma ngati sutsagana nane, sindipita.” 9 Pamenepo Debora anati: “Sindilephera, tipitira limodzi. Ngakhale zili choncho, ulemerero sukhala wako kumene ukupitako, chifukwa Yehova adzapereka Sisera m’manja mwa munthu wamkazi.”+ Atatero, Debora ananyamuka n’kutsagana ndi Baraki ku Kedesi.+ 10 Ndipo Baraki anasonkhanitsa pamodzi fuko la Zebuloni+ ndi fuko la Nafitali ku Kedesi, moti amuna 10,000 anam’tsatira,+ ndipo Debora nayenso anapita nawo.

11 Zili choncho, Hiberi+ Mkeni anapatukana ndi Akeni,+ ana a Hobabu mpongozi wa Mose,+ ndipo anamanga hema wake pafupi ndi mtengo waukulu ku Zaananimu, ku Kedesi.

12 Ndiyeno kunafika uthenga kwa Sisera, wonena kuti Baraki, mwana wa Abinowamu,+ wapita kuphiri la Tabori.+ 13 Nthawi yomweyo, Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ankhondo, magaleta 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo.+ Anasonkhanitsanso anthu ake onse kuchokera ku Haroseti-ha-goimu, kupita kuchigwa cha Kisoni.+ 14 Kenako Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka, pakuti lero ndi tsiku limene Yehova adzapereka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.”+ Ndipo Baraki anatsikadi m’phiri la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatira. 15 Pamenepo Yehova anayamba kusokoneza+ ndi kuwononga Sisera ndi magaleta ake onse ankhondo, pamodzi ndi anthu ake onse. Anawasokoneza ndi kuwawononga ndi lupanga pamaso pa Baraki. Zitatero Sisera anatsika m’galeta wake n’kuyamba kuthawa wapansi. 16 Baraki anathamangitsa+ magaleta ankhondowo+ ndi gulu lonselo mpaka ku Haroseti-ha-goimu, moti gulu lonse la Sisera linaphedwa ndi lupanga. Sipanatsale ndi mmodzi yemwe.+

17 Koma Sisera+ anathawa wapansi kupita kuhema wa Yaeli,+ mkazi wa Hiberi Mkeni,+ pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori+ ndi nyumba ya Hiberi Mkeni. 18 Pamenepo Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndi kumuuza kuti: “Bwerani kuno, mbuyanga, bwerani kuno kwathu. Musaope ayi.” Choncho anapatuka kukalowa m’hema wa Yaeli. Pambuyo pake, anam’funditsa bulangete. 19 Kenako Sisera anamuuza kuti: “Ndipatseko madzi akumwa, chifukwa ndili ndi ludzu.” Pamenepo anatsegula thumba lachikopa+ la mkaka ndi kum’patsa kuti amwe.+ Atatero, anam’funditsanso. 20 Ndipo Sisera anauza Yaeli kuti: “Uime pakhomo la hema, ndipo pakabwera munthu n’kukufunsa kuti, ‘Kodi pali mwamuna pano?’ umuuze kuti, ‘Palibe.’”

21 Ndiyeno Yaeli mkazi wa Hiberi anatenga chikhomo cha hema ndi nyundo. Kenako analowa m’hemamo, akuyenda monyang’ama n’kukhoma chikhomocho m’mutu mwa Sisera pafupi ndi khutu,+ mpaka chikhomocho chinalowa pansi. Apa n’kuti Sisera ali m’tulo tofa nato ndiponso ali wotopa kwambiri. Mmenemu ndi mmene Sisera anafera.+

22 Pa nthawiyi, Baraki anatulukira akusakasaka Sisera. Pamenepo Yaeli anapita kukamuchingamira, ndipo anamuuza kuti: “Tabwerani ndikuonetseni munthu amene mukum’funafunayo.” Iye anam’tsatira, ndipo anangoona Sisera ali thasa pansi wakufa, chikhomo chili m’mutu mwake pafupi ndi khutu.

23 Umu ndi mmene Mulungu anagonjetsera+ Yabini mfumu ya Kanani, pamaso pa ana a Isiraeli pa tsiku limenelo. 24 Ndipo dzanja la ana a Isiraeli linakulirakulirabe mphamvu popanikiza Yabini mfumu ya Kanani,+ mpaka anapha Yabini mfumu+ ya Kanani.

5 Pa tsiku limenelo, Debora+ ndi Baraki+ mwana wa Abinowamu,+ anayamba kuimba nyimbo,+ ndipo anati:

 2 “Posunga tsitsi lalitali mu Isiraeli monga lumbiro la nkhondo,

Chifukwa cha kudzipereka mwaufulu kwa anthu,+

Tamandani Yehova.+

 3 Mvetserani mafumu inu,+ inunso nduna, tcherani khutu:

Ine ndidzaimbira Yehova, ndithu ndidzamuimbira.

Ndidzaimbira Yehova, Mulungu wa Isiraeli,+ nyimbo zomutamanda.+

 4 Yehova, pamene munayenda kuchokera ku Seiri,+

Pamene munaguba kuchokera kudera la Edomu,+

Dziko linagwedezeka,+ kumwamba kunagwetsa madzi,+

Mitambo inagwetsa madzi.

 5 Mapiri anasungunuka ndi kuyenda ngati madzi, kuchoka pamaso pa Yehova,+

Sinai+ uyu anayenda ngati madzi kuchoka pamaso pa Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli.+

 6 M’masiku a Samagara+ mwana wa Anati,

M’masiku a Yaeli,+ m’njira munalibe odutsamo,

Ndipo oyenda m’misewu anayamba kuyenda njira zolambalala.+

 7 Anthu okhala m’midzi anachoka m’midzi yawo, anachoka m’midzi ya Isiraeli,+

Kufikira pamene ine Debora+ ndinauka,

Kufikira pamene ine ndinauka monga mayi mu Isiraeli.+

 8 Anayamba kusankha milungu yatsopano.+

Atatero m’pamene nkhondo inafika m’mizinda.+

Panalibe chishango kapena mkondo waung’ono,

Pakati pa anthu 40,000 mu Isiraeli.+

 9 Mtima wanga uli pa atsogoleri a asilikali a Isiraeli,+

Amene anadzipereka mwaufulu pakati pa anthu awo.+

Tamandani Yehova.+

10 Inu okwera abulu ofiirira,+

Inu okhala pansalu zokwera mtengo,

Ndi inu oyenda mumsewu,

Ganizirani ntchito za Mulungu izi:+

11 Mawu a anthu ena otunga madzi anamveka pamalo otungira madzi,+

Kumeneko anayamba kusimba ntchito zolungama za Yehova,+

Anasimba ntchito zolungama za anthu ake okhala m’midzi ya Isiraeli.

Atatero m’pamene anthu a Yehova anapita kumizinda.

12 Dzuka! Dzuka Debora iwe!+

Dzuka! Dzuka! Imba nyimbo!+

Imirira Baraki iwe!+ Tsogolera anthu ogwidwa, iwe mwana wa Abinowamu.+

13 Pamenepo, opulumuka anapita kwa anthu otchuka.

Anthu a Yehova anabwera kwa ine, pokalimbana ndi amphamvu.

14 Amene anali m’chigwa anachokera m’fuko la Efuraimu,+

Ndipo iwo anali ndi iwe Benjamini, pakati pa anthu a mtundu wako.

Atsogoleri a asilikali anachokera kwa Makiri,+

Ndipo osunga zida za mlembi, anachokera m’fuko la Zebuloni.+

15 Akalonga a fuko la Isakara+ anali ndi Debora,

Mmene anachitira Isakara, ndi mmenenso anachitira Baraki.+

Anamutumiza kuchigwa akuyenda wapansi.+

Pakati pa magulu a m’fuko la Rubeni, panali kufufuza mozama za mumtima.+

16 Unakhaliranji pansi pakati pa zikwama ziwiri za pachishalo,

N’kumamvetsera nyimbo za zitoliro zoimbira nkhosa?+

Pakuti m’magulu a fuko la Rubeni munali kufufuza mozama za mumtima.+

17 Anthu a ku Giliyadi anakhalabe kwawo komweko, kutsidya lina la Yorodano.+

Ndipo n’chifukwa chiyani Dani anakhalabe m’zombo kwa kanthawi?+

Aseri anangokhala phee pagombe la nyanja,

Nakhalabe pamadoko ake.+

18 Anthu a m’fuko la Zebuloni ndiwo anatonza miyoyo yawo mpaka kuiika pangozi.+

Anthu a m’fuko la Nafitali+ nawonso anachita zomwezo m’mapiri a dziko.+

19 Mafumu anabwera ndi kumenya nkhondo.

Pamenepo mafumu a Kanani anamenya nkhondo,+

Anamenya nkhondo ku Taanaki,+ pafupi ndi madzi a ku Megido.+

Iwo sanapezepo phindu la siliva.+

20 Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba,+

Zinamenyana ndi Sisera zili m’njira zawo.

21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,+

Mtsinje wakalekale, mtsinje wa Kisoni.+

Moyo wangawe, unapondereza adani amphamvu.+

22 Pamenepo ziboda za mahatchi* zinaguguda pansi,+

Chifukwa cha kuthamangathamanga kwa mahatchiwo.

23 Mngelo wa Yehova+ anati: ‘Tembererani+ Merozi,

Tembererani anthu ake mosaleka,

Chifukwa sanathandize Yehova,

Sanabwere ndi anthu amphamvu kudzathandiza Yehova.’

24 Yaeli,+ mkazi wa Hiberi Mkeni,+ akhale wodalitsika pakati pa akazi onse,

Akhale wodalitsika pakati pa akazi onse okhala m’mahema.+

25 Sisera anapempha madzi, Yaeli anapereka mkaka.

Anamupatsa mkaka, m’mbale yolowa yaikulu yomwera anthu olemekezeka pa phwando.+

26 Kenako anatambasula dzanja lake ndi kugwira chikhomo cha hema.

Anatambasulanso dzanja lake lamanja ndi kutenga nyundo yamtengo, ya anthu ogwira ntchito mwamphamvu.+

Atatero anakhoma Sisera m’mutu ndipo chikhomocho chinatulukira mbali ina ya mutu wakewo.+

Anaphwanya ndi kudula fupa la pafupi ndi khutu la Sisera.

27 Sisera anakomoka, kugwa ndi kugona pakati pa mapazi ake,

Iye anakomoka n’kugwa.

Pamene anakomokerapo, anagwera pomwepo, atagonja.+

28 Munthu wamkazi anaima pawindo ndi kuyang’ana kunja, kumuyembekezera,

Amayi a Sisera anayang’ana kunja pawindo,*+ kumuyembekezera, ndipo anati,

‘N’chifukwa chiyani galeta lake lankhondo lachedwa kubwera?+

N’chifukwa chiyani kuguguda kwa magaleta ake kwachedwa kumveka?’+

29 Akazi anzeru pakati pa gulu la amayi ake olemekezeka+ anali kumuyankha,

Iyenso n’kumadziyankhira mumtima mwake, kuti,

30 ‘Kodi sanapeze zofunkha ndipo ayenera kuzigawa?+

Kodi sayenera kugawa mkazi mmodzi, kapenanso akazi awiri kwa mwamuna aliyense wamphamvu,+

Ndi nsalu za Sisera zofunkhidwa zonyika mu utoto, ndithu nsalu zofunkhidwa zonyika mu utoto?

Kodi sayenera kugawa chovala chopeta chonyika mu utoto, inde, zovala ziwiri zopeta,

Kuti amuna ofunkha avale m’makosi awo?’

31 Inu Yehova, adani anu onse afafanizidwe chimodzimodzi,+

Ndipo okukondani inu+ akhale amphamvu ngati mmene dzuwa limakhalira.”+

Choncho, dzikolo linakhala pa mtendere zaka 40.+

6 Kenako ana a Isiraeli anayamba kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Motero Yehova anawapereka m’manja mwa Amidiyani+ kwa zaka 7. 2 Amidiyaniwo anayamba kusautsa Aisiraeli.+ Chifukwa cha kusautsidwa ndi Amidiyani kumeneku, ana a Isiraeli anadzikonzera malo apansi osungiramo zinthu m’mapiri. Anadzikonzeranso mapanga ndi malo ena ovuta kufikako kuti azithawirako.+ 3 Ndiyeno Aisiraeli akalima minda yawo,+ Amidiyani, Aamaleki+ ndi anthu a Kum’mawa+ anali kubwera kudzawaukira. 4 Anali kuwazungulira ndi kuwawonongera zokolola zawo zonse mpaka kukafika ku Gaza. Sanali kuwasiyira chakudya chilichonse ngakhalenso nkhosa, ng’ombe kapena bulu mu Isiraeli.+ 5 Iwo anali kubwera ndi ziweto zawo ndi mahema awo. Anali kubwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Iwo anali kubwera m’dzikomo n’kumaliwononga.+ 6 Choncho Aisiraeli anasautsika kwadzaoneni chifukwa cha Amidiyani. Pamenepo, ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+

7 Ana a Isiraeli atafuulira Yehova kuti awathandize chifukwa cha Amidiyani,+ 8 Yehova anatumiza munthu wina, mneneri,+ kwa ana a Isiraeli, ndipo anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndine amene ndinakutulutsani mu Iguputo,+ m’nyumba yaukapolo.+ 9 Choncho ndinakulanditsani m’manja mwa Iguputo ndiponso m’manja mwa onse amene anali kukuponderezani, ndipo ndinapitikitsa adani anu pamaso panu ndi kukupatsani dziko lawo.+ 10 Komanso ndinakuuzani kuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Musaope milungu ya Aamori+ amene mukukhala m’dziko lawo.”+ Koma inu simunamvere mawu anga.’”+

11 Kenako, kunabwera mngelo wa Yehova+ ndi kukhala pansi pa mtengo waukulu umene unali ku Ofira. Mtengo umenewu unali wa Yowasi, Mwabi-ezeri.+ Pa nthawiyi, Gidiyoni+ mwana wa Yowasi, anali kupuntha tirigu moponderamo mphesa kuti akamubise mwamsanga Amidiyani asanaone. 12 Pamenepo mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye, ndipo anati: “Yehova ali ndi iwe,+ munthu wolimba mtima ndi wamphamvuwe.” 13 Ndiyeno Gidiyoni anayankha kuti: “Pepani mbuyanga, koma ngati Yehova ali ndi ife, n’chifukwa chiyani zonsezi zatigwera?+ Nanga ntchito zake zodabwitsa zija,+ zimene makolo athu anatisimbira zili kuti?+ Iwo anatiuza kuti, ‘Yehova ndiye anatitulutsa mu Iguputo.’+ Koma tsopano Yehova watisiya,+ ndipo watipereka m’manja mwa Amidiyani.” 14 Atatero, Yehova anamuyang’ana ndi kunena kuti: “Pita ndi mphamvu zimene ndakupatsazi,+ ndipo udzapulumutsadi Isiraeli m’manja mwa Amidiyani.+ Si ine amene ndakutuma kodi?”+ 15 Koma iye anayankha kuti: “Pepani Yehova. Kodi Isiraeli ndidzam’pulumutsa ndi chiyani?+ Pajatu banja lathu* ndilo laling’ono zedi m’fuko lonse la Manase, ndipo m’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambiri ndine.”+ 16 Koma Yehova anamuuza kuti: “Popeza ndidzakhala ndi iwe,+ udzaphadi Amidiyani+ ngati kuti ukupha munthu mmodzi.”

17 Pamenepo iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima,+ mundisonyeze chizindikiro kuti nditsimikize kuti ndinudi amene mukulankhula nane.+ 18 Chonde musachoke, kufikira nditabwera+ ndi kukupatsani mphatso yanga.”+ Choncho iye anati: “Ineyo ndikhalabe pompano kufikira utabweranso.” 19 Ndiyeno Gidiyoni analowa m’nyumba ndi kuphika nyama ya mwana wa mbuzi.+ Anatenganso ufa wokwana muyezo umodzi wa efa* ndi kupanga mikate yopanda chofufumitsa.+ Atatero, anatenga nyamayo ndi kuiika m’dengu, ndipo msuzi anauika mumphika. Kenako, anatenga zinthu zimenezi ndi kukamupatsa mngelo uja pansi pa mtengo waukulu uja.

20 Pamenepo mngelo wa Mulungu woona anamuuza kuti: “Tenga nyamayi ndi mikate yopanda chofufumitsayo, ndi kuziika pamwala waukuluwo,+ ndipo ukhuthule msuziwo.” Gidiyoni anachitadi zomwezo. 21 Atatero, mngelo wa Yehova anatambasula dzanja lake, ndipo anakhudza nyama ndi mikate yopanda chofufumitsayo ndi nsonga ya ndodo imene inali m’dzanja lake. Pamenepo, moto wotuluka m’mwalawo unayamba kulilima, n’kunyeketsa nyama ndi mkate wopanda chofufumitsawo,+ koma mngelo wa Yehova anazimiririka. 22 Tsopano Gidiyoni anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova.+

Nthawi yomweyo Gidiyoni anati: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Ndaonana ndi mngelo wa Yehova maso ndi maso.”+ 23 Koma Yehova anamuuza kuti: “Mtendere ukhale nawe.+ Usachite mantha.+ Suufa.”+ 24 Choncho, Gidiyoni anamangira Yehova guwa lansembe+ pamenepo, ndipo limatchedwa+ Yehova-salomu* kufikira lero. Guwalo lili ku Ofira,+ mzinda wa Aabi-ezeri, mpaka pano.

25 Ndiyeno zinachitika kuti usiku womwewo, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Tenga ng’ombe yaing’ono yamphongo ya bambo ako, ng’ombe yachiwiri yazaka 7 ija. Kenako ugwetse guwa lansembe la Baala+ la bambo ako ndipo udule mzati wopatulika umene uli pafupi ndi guwalo.+ 26 Ndipo umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe mwa kuyala miyala. Ulimange pamwamba pa linga la malo otetezekawa. Ukatero, utenge ng’ombe yaing’ono yamphongo yachiwiri ija, ndi kuipereka monga nsembe yotentha ndi moto pankhuni za mzati wopatulika umene udulewo.” 27 Choncho Gidiyoni anatenga amuna 10 mwa atumiki ake ndi kuchita zonse zimene Yehova anamuuza.+ Koma chifukwa choopa kwambiri anthu a m’nyumba ya bambo ake ndi anthu a mumzindawo, anachita zimenezi usiku osati masana.+

28 Amuna a mumzindawo atadzuka m’mawa kwambiri monga mwa nthawi zonse, anangoona kuti guwa lansembe la Baala lagwetsedwa, ndipo mzati wopatulika+ umene unali pambali pake wadulidwa. Iwo anaonanso kuti paguwa lansembe latsopano limene lamangidwa, panali pataperekedwa ng’ombe yaing’ono yamphongo yachiwiri ija. 29 Ndiyeno anayamba kufunsana kuti: “Ndani wachita zimenezi?” Choncho anayamba kufufuza ndi kufunafuna amene anachita zimenezo. Pamapeto pake iwo anati: “Ndi Gidiyoni, mwana wa Yowasi amene wachita zimenezi.” 30 Pamenepo amuna a mumzindawo anauza Yowasi kuti: “Tulutsa mwana wako kuti timuphe,+ chifukwa wagwetsa guwa lansembe la Baala ndi kudula mzati wopatulika umene unali pambali pake.” 31 Koma Yowasi+ anauza onse amene anamuukirawo kuti:+ “Kodi inu mungaweruzire Baala mlandu kuti mum’pulumutse? Aliyense womuweruzira mlandu ayenera kuphedwa m’mawa womwe uno.+ Ngati Baalayo ndi Mulungu,+ adziweruzire yekha mlanduwu,+ chifukwa wina wake wagwetsa guwa lake lansembe.” 32 Choncho Yowasi anatcha Gidiyoni dzina lakuti Yerubaala*+ pa tsiku limenelo, ndipo anati: “Baala adziweruzire yekha mlandu, chifukwa winawake wagwetsa guwa lake lansembe.”+

33 Ndiyeno Amidiyani+ ndi Aamaleki onse,+ pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa+ anasonkhana pamodzi+ ndi kuwoloka mtsinje, ndipo anamanga msasa wawo m’chigwa cha Yezereeli.+ 34 Zitatero, Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova,+ moti anayamba kuliza lipenga+ la nyanga ya nkhosa ndipo Aabi-ezeri+ anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira. 35 Iye anatumiza mithenga+ m’dera lonse la fuko la Manase, ndipo anthu a m’fuko limeneli nawonso anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira. Anatumizanso mithenga m’madera onse a mafuko a Aseri, Zebuloni ndi Nafitali, ndipo nawonso anabwera kudzakumana naye.

36 Tsopano Gidiyoni anauza Mulungu woona kuti: “Kuti ndidziwe kuti mudzapulumutsa Isiraeli kudzera mwa ine, monga mmene mwalonjezera,+ 37 ndiika ubweya wa nkhosa pansi, pamalo opunthira mbewu. Ngati mame angagwe paubweya wokhawu, koma nthaka yonse n’kukhala youma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsadi Isiraeli kudzera mwa ine, monga mmene mwalonjezera.” 38 Ndipo zinachitikadi momwemo. Atadzuka m’mawa kwambiri tsiku lotsatira n’kufinya ubweya wa nkhosawo, ubweyawo unatulutsa madzi ochuluka oti n’kudzaza chikho chachikulu cha pa phwando. 39 Komabe, Gidiyoni anauza Mulungu woona kuti: “Mkwiyo wanu usandiyakire chonde, ndiloleni ndilankhulenso kamodzi kokhaka. Ndiloleni chonde, ndikuyeseninso kamodzi kokha ndi ubweyawu, kuti nditsimikizire za nkhaniyi. Nthaka yonse ikhathamire ndi mame, koma ubweya wokhawu ukhale wouma.” 40 Choncho, Mulungu anachitadi zimenezo usiku umenewo. Nthaka yonse inakhathamira ndi mame, koma ubweya wokhawo unali wouma.

7 Pamenepo Yerubaala,+ kapena kuti Gidiyoni,+ pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, anadzuka m’mawa kwambiri ndi kumanga msasa pachitsime cha Harodi. Msasa wa Amidiyani unali chakumpoto, m’chigwa, kuphiri la More. 2 Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene uli nawowa ndi ochuluka kwambiri kuti ndipereke Amidiyani m’manja mwawo,+ chifukwa mwina Isiraeli angadzitukumule+ pamaso panga ndi kunena kuti, ‘Ndinadzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.’+ 3 Tsopano lengeza ndipo anthu onse amve, kuti, ‘Alipo kodi akuchita mantha ndi kunjenjemera? Abwerere.’”+ Choncho ndi mawu amenewa, Gidiyoni anayesa anthuwo. Pamenepo, anthu 22,000 anabwerera ndipo panatsala anthu 10,000.

4 Komabe, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene atsalawa ndi ochulukabe.+ Pita nawo kumadzi kuti ndikawayese kumeneko. Ndiyeno amene ndidzakuuza kuti, ‘Uyu apite nawe,’ ameneyo apite nawe, koma aliyense amene ndidzakuuza kuti, ‘Uyu asapite nawe,’ ameneyo asapite nawe.” 5 Choncho Gidiyoni anauza anthuwo kuti apite kumadzi.+

Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Aliyense amene akamwe madzi potunga madziwo ndi manja n’kumamwera m’manjamo, ukamuike kumbali ina. Ndipo aliyense amene pakumwa madzi akawerame n’kugwada,+ ukamuike kumbali inanso.” 6 Ndipo anthu amene anamwa madzi ndi manja anakwana 300. Koma ena onse anamwa atawerama n’kugwada.

7 Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Ndidzapulumutsa anthu inu pogwiritsa ntchito amuna 300 amene anamwa madzi ndi manja awo, ndipo ndidzapereka Amidiyani m’manja mwanu.+ Koma ena onsewa, aliyense abwerere kwawo.” 8 Choncho, iye anabweza amuna onse a Isiraeli koma anatsala ndi amuna 300 aja. Amenewa anatenga chakudya ndi malipenga a nyanga ya nkhosa+ m’manja mwa anthu amene anali kubwerera kwawo. Apa n’kuti msasa wa Amidiyani uli kumunsi kwawo, m’chigwa.+

9 Ndiyeno usiku umenewo,+ Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Nyamuka, pita kumsasa wa Amidiyani ndi kuuthira nkhondo, chifukwa ndaupereka m’manja mwako.+ 10 Koma ngati ukuchita mantha kupita kumsasawo, choyamba upiteko ndi Pura, mtumiki wako.+ 11 Kumeneko ukamvetsere zolankhula zawo.+ Pambuyo pake udzalimba mtima+ ndipo udzapitadi kumsasawo ndi kuuthira nkhondo.” Pamenepo, Gidiyoni ndi Pura mtumiki wake, anapita kumunsi pafupi kwambiri ndi asilikali amene anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo amene anali mumsasawo.

12 Tsopano Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa,+ anaphimba chigwa chonse chifukwa cha kuchuluka kwawo ngati dzombe.+ Ngamila zawo+ zinali zosawerengeka, zochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja. 13 Tsopano Gidiyoni anafika kumsasawo ndipo anangomva munthu akusimbira mnzake zimene analota, kuti: “Tamvera zimene ndalota ine.+ Ndalota mtanda wa mkate wa balere wozungulira ukugubuduzika kubwera mumsasa wa Amidiyani. Mtandawo unafika pahema lina ndi kuliwomba moti hemalo linagwa.+ Kenako mtandawo unagadabuza hemalo n’kuliphwasula.” 14 Pamenepo mnzakeyo anayankha+ kuti: “Si china ayi. Imeneyi ndi nkhondo ya Gidiyoni+ mwana wa Yowasi, mwamuna wa ku Isiraeli. Mulungu woona+ wapereka Amidiyani ndi msasa wathu wonse m’manja mwake.”+

15 Gidiyoni atangomva lotolo ndi tanthauzo lake,+ analambira Mulungu.+ Kenako anabwerera kumsasa wa Isiraeli ndi kuwauza kuti: “Tiyeni,+ pakuti Yehova wapereka msasa wa Amidiyani m’manja mwanu.” 16 Ndiyeno amuna 300 aja anawagawa m’magulu atatu. Aliyense anamupatsa lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi mtsuko waukulu wopanda kanthu, ndipo m’mitsukomo anaikamo miyuni. 17 Kenako anawauza kuti: “Muonetsetse ndi kuphunzira pa zimene ine ndikuchita, ndipo nanunso muchite zomwezo. Ndikakafika m’malire a msasa, zimene ine ndikachite, nanunso mukachite zomwezo. 18 Ine ndikaliza lipenga la nyanga ya nkhosa pamodzi ndi anthu onse a m’gulu langa, nanunso mulize malipenga anu kuzungulira msasa wonse,+ ndipo munene kuti, ‘Nkhondo ya Yehova+ ndi ya Gidiyoni!’”

19 Chotero Gidiyoni anafika kumalire a msasa pamodzi ndi amuna 100 amene anali naye. Apa n’kuti ulonda wapakati pa usiku*+ ukungoyamba kumene, ndipo anali atangosintha kumene alonda a msasa. Pamenepo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ ndi kuswa mitsuko yaikulu imene inali m’manja mwawo.+ 20 Ndipo magulu atatuwo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ ndi kuphwanya mitsuko ikuluikulu ija. Atatero ananyamulanso miyuni ndi dzanja lawo lamanzere ndipo malipenga anali m’dzanja lawo lamanja, n’kuyamba kufuula kuti: “Nkhondo ya Yehova+ ndi ya Gidiyoni!” 21 Pa nthawi imeneyi aliyense anaimirirabe pamalo ake kuzungulira msasa wonsewo, ndipo mumsasa wonse wa Amidiyani munali chipwirikiti, anthu anali kufuula ndi kuthawa.+ 22 Amuna 300+ aja anapitiriza kuliza malipenga,+ ndipo Yehova anachititsa Amidiyani kuukirana okhaokha mumsasa wonsewo.+ Anthu onse a mumsasawo anathawa mpaka kukafika ku Beti-sita, ndi ku Zerera mpaka kumalire kwa mzinda wa Abele-mehola+ pafupi ndi Tabati.

23 Pa nthawiyi anasonkhanitsa pamodzi amuna a mu Isiraeli kuchokera m’madera a mafuko a Nafitali,+ Aseri+ ndi Manase+ yense, ndipo anapitikitsa+ Amidiyani. 24 Ndiyeno Gidiyoni anatumiza amithenga kudera lonse lamapiri la Efuraimu,+ kuti: “Pitani mofulumira ku Beti-bara ndi kumtsinje wa Yorodano, ndipo mukaike amuna m’malo owolokera kuti Amidiyani asadutse.” Choncho, amuna onse a Efuraimu anasonkhana pamodzi ndipo anatseka malo owolokera Yorodano ndi mitsinje yake ing’onoing’ono+ mpaka ku Beti-bara. 25 Anagwiranso akalonga awiri a Amidiyani, Orebi ndi Zeebi.+ Atatero, anapha Orebi pathanthwe la Orebi,+ ndipo Zeebi anamuphera pamalo opondera mphesa a Zeebi. Iwo anapitirizabe kuthamangitsa Amidiyani,+ kenako anabweretsa mutu wa Orebi ndi Zeebi kwa Gidiyoni m’chigawo cha Yorodano.+

8 Pamenepo amuna a ku Efuraimu anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani watichitira zimenezi? Bwanji sunatiitane pokamenya nkhondo ndi Amidiyani?”+ Ndipo iwo anayesetsa mwamphamvu kuti achite naye mkangano.+ 2 Chotero iye anawayankha kuti: “Kodi ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?+ Kodi zokunkha za Efuraimu+ si zabwino kwambiri kuposa mphesa zimene Abi-ezeri+ wakolola? 3 Kodi Mulungu sanapereke Orebi ndi Zeebi,+ akalonga a Midiyani m’manja mwanu? Ndipo ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?” Atanena mawu amenewa, mkwiyo wawo unaphwa.+

4 Kenako, Gidiyoni anafika ku Yorodano n’kuwoloka mtsinjewo pamodzi ndi amuna 300 amene anali nawo aja, ali otopa koma akuthamangitsabe adaniwo. 5 Ndiyeno iye anapempha amuna a ku Sukoti+ kuti: “Chonde, patsaniko anthu amene akunditsatirawa+ mitanda yobulungira ya mkate chifukwa ndi otopa, pakuti ndikuthamangitsa Zeba+ ndi Zalimuna,+ mafumu a Midiyani.” 6 Koma poyankha, akalonga a ku Sukoti anati: “Tipatsirenji asilikali ako mkate ngati kuti wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?”+ 7 Pamenepo Gidiyoni anawauza kuti: “N’chifukwa chake Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna m’manja mwanga, ndithu, ndidzakukwapulani ndi mitengo yaminga ya m’chipululu komanso ndi zitsamba zaminga.”+ 8 Choncho anapitiriza ulendo wake kuchoka kumeneko n’kupita ku Penueli.+ Atafika ku Penueli, anawapemphanso chimodzimodzi, koma amuna a kumeneko anamuyankha mofanana ndi mmene amuna a ku Sukoti anamuyankhira. 9 Zitatero, anauzanso amuna a ku Penueli kuti: “Ndikabwerako bwino, ndidzagwetsa nsanja yanuyi.”+

10 Pamenepa n’kuti Zeba ndi Zalimuna+ ali ku Karikori pamodzi ndi asilikali awo okwana pafupifupi 15,000. Asilikaliwa ndi amene anatsala pa gulu lonse la asilikali a Kum’mawa,+ ndipo amene anali ataphedwa anali asilikali 120,000.+ 11 Gidiyoni anayendabe panjira ya anthu okhala m’mahema, mpaka kukafika kum’mawa kwa Noba ndi Yogebeha.+ Kumeneko anathira nkhondo msasa wa adaniwo iwo asanakonzekere.+ 12 Zeba ndi Zalimuna atathawa, iye mosazengereza anawathamangitsa mpaka kuwagwira mafumu a Midiyaniwa.+ Atatero, anachititsa gulu lawo lonse kunjenjemera ndi mantha.

13 Ndiyeno Gidiyoni mwana wa Yowasi anayamba kubwerera kuchokera kunkhondo, podzera njira yopita ku Heresi. 14 Ali m’njira, anagwira mnyamata wa ku Sukoti+ amene anam’funsa mafunso.+ Pamenepo, mnyamatayo analembera Gidiyoni mayina okwana 77 a akalonga+ ndi akulu a mzinda wa Sukoti. 15 Choncho, Gidiyoni anapita kwa amuna a mumzinda wa Sukoti ndi kuwauza kuti: “Kodi Zeba ndi Zalimuna si awa? Aja amene munandinyoza nawo ponena kuti, ‘Tipatsirenji anyamata ako otopawo mkate ngati kuti wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?’”+ 16 Ndiyeno anatenga akulu a mzindawo, n’kutenganso mitengo yaminga ya m’chipululu ndi zitsamba zaminga. Atatero, anaonetsa amuna a ku Sukotiwo zoopsa.+ 17 Anagwetsanso+ nsanja ya ku Penueli+ ija, ndi kupha amuna a mumzindawo.

18 Tsopano Gidiyoni anafunsa Zeba ndi Zalimuna+ kuti: “Kodi amuna amene munapha ku Tabori+ anali otani?” Poyankha iwo anati: “Iwo anali ngati iweyo. Maonekedwe ake aliyense wa iwo anali ngati mwana wa mfumu.” 19 Pamenepo Gidiyoni anawauza kuti: “Anali abale anga, ana a amayi anga. Pali Yehova Mulungu wamoyo, sindikanakuphani mukanawasiya amoyo.”+ 20 Ndiyeno anauza Yeteri mwana wake woyamba kuti: “Nyamuka uwaphe.” Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake chifukwa anachita mantha, pakuti anali akali wamng’ono.+ 21 Choncho Zeba ndi Zalimuna anati: “Nyamuka iweyo utiphe wekha. Munthu amakhala ndi mphamvu+ zolingana ndi msinkhu wake.” Motero Gidiyoni ananyamuka ndi kupha+ Zeba ndi Zalimuna, ndipo anatenga zokongoletsa zooneka ngati mwezi zimene zinali pakhosi la ngamila zawo.

22 Kenako amuna a Isiraeli anauza Gidiyoni kuti: “Ukhale wotilamulira wathu,+ iweyo, mwana wako ndi mdzukulu wako, chifukwa watipulumutsa m’manja mwa Amidiyani.”+ 23 Koma Gidiyoni anawayankha kuti: “Ineyo sindikhala wokulamulirani, ngakhalenso mwana wanga sakhala wokulamulirani.+ Yehova ndiye azikulamulirani.”+ 24 Ndipo anawauzanso kuti: “Ndikupempheni chinthu chimodzi: Aliyense wa inu andipatse ndolo* yapamphuno+ kuchokera pa zimene wafunkha.” (Ogonjetsedwawo anali ndi ndolo zapamphuno zagolide, chifukwa anali Aisimaeli.)+ 25 Pamenepo iwo anati: “Sitilephera, tipereka.” Atatero anafunyulula nsalu, ndipo aliyense anaponyapo ndolo yapamphuno kuchokera pa zimene anafunkha. 26 Kulemera kwa ndolo zapamphuno zagolide zimene anapempha, kunali masekeli* agolide 1,700, osawerengera zokongoletsa zooneka ngati mwezi,+ ndolo ndi zovala zaubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ zimene mafumu a Midiyani aja anali atavala, osawerengeranso mikanda imene inali pakhosi la ngamila zawo.+

27 Ndiyeno Gidiyoni anagwiritsa ntchito golideyo popanga chovala cha efodi,+ chimene anachisonyeza kwa anthu mumzinda wakwawo wa Ofira.+ Pamenepo Isiraeli yense anayamba kuchilambira ngati fano,*+ moti chinakhala msampha kwa Gidiyoni ndi nyumba yake.+

28 Choncho, Amidiyani+ anagonjetsedwa ndi ana a Isiraeli, ndipo Amidiyani sanakwezenso mutu wawo. Zitatero, dziko linakhala pa mtendere zaka 40 m’masiku a Gidiyoni.+

29 Ndipo Yerubaala,*+ mwana wa Yowasi, anabwerera kwawo ndipo anapitirizabe kukhala kunyumba kwake.

30 Gidiyoni anakhala ndi ana 70+ otuluka m’chiuno mwake, chifukwa anadzakhala ndi akazi ambiri. 31 Nayenso mdzakazi* wake wa ku Sekemu, anamubalira mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lakuti Abimeleki.+ 32 M’kupita kwa nthawi, Gidiyoni mwana wa Yowasi anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino ndi wautali, ndipo anamuika m’manda a Yowasi bambo ake, mumzinda wa Ofira wa Aabi-ezeri.+

33 Ndiyeno zinachitika kuti Gidiyoni atangomwalira, ana a Isiraeli anayambanso kupembedza Abaala,+ moti anaika Baala-beriti* kukhala mulungu wawo.+ 34 Ana a Isiraeliwo sanakumbukire Yehova Mulungu wawo,+ amene anawalanditsa m’manja mwa adani awo onse owazungulira,+ 35 ndipo sanasonyeze kukoma mtima kosatha+ kwa anthu a m’nyumba ya Yerubaala, kapena kuti Gidiyoni, pa zabwino zonse zimene iye anachitira Isiraeli.+

9 Patapita nthawi, Abimeleki+ mwana wa Yerubaala, anapita ku Sekemu+ kwa abale a mayi ake. Kumeneko anayamba kulankhula nawo ndiponso kulankhula ndi banja lonse la bambo a mayi akewo kuti: 2 “Chonde lankhulani nzika zonse za Sekemu zikumva, kuti, ‘Chabwino n’chiti kwa inu, kuti amuna 70,+ ana onse a Yerubaala akulamulireni, kapena munthu mmodzi akulamulireni? Ndipotu kumbukirani kuti ine ndine fupa lanu ndi mnofu wanu.’”+

3 Choncho abale a mayi ake anayamba kulankhula mawu onsewa nzika zonse za Sekemu zikumva, moti mitima yawo inakonda Abimeleki,+ chifukwa anati: “Ndi m’bale wathu ameneyu.”+ 4 Kenako iwo anatenga ndalama zasiliva 70 m’kachisi wa Baala-beriti+ ndi kum’patsa. Ndalama zimenezi Abimeleki analembera ganyu anthu osowa ntchito ndi achipongwe+ kuti azim’tsatira. 5 Atatero anapita kunyumba ya bambo ake ku Ofira+ ndi kupha abale ake,+ ana aamuna 70 a Yerubaala, pamwala umodzi. Koma sanaphe Yotamu, mwana wamng’ono kwambiri mwa ana aamuna a Yerubaala, chifukwa anali atabisala.

6 Kenako nzika zonse za Sekemu ndi anthu onse m’nyumba ya Milo+ anasonkhana pamodzi kumene kunali chipilala pafupi ndi mtengo waukulu+ ku Sekemu.+ Kumeneko analonga Abimeleki ufumu.+

7 Yotamu atauzidwa zimene zinachitikazo, nthawi yomweyo anapita pamwamba pa phiri la Gerizimu+ ndi kulankhula nawo mofuula kuti: “Ndimvereni, inu nzika za Sekemu, ndipo Mulungu akumvereni:

8 “Kalekale mitengo inafuna kudzoza mfumu yawo. Pamenepo mitengoyo inauza mtengo wa maolivi+ kuti, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’+ 9 Koma mtengo wa maoliviwo unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye kutulutsa mafuta amene amagwiritsidwa ntchito potamanda+ Mulungu ndi anthu, n’kupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’+ 10 Kenako mitengoyo inauza mtengo wa mkuyu+ kuti, ‘Bwera kuno, ukhale mfumu yathu.’ 11 Koma mtengo wa mkuyuwo unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye kukoma kwanga ndi zipatso zanga zabwinozi, n’kupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’+ 12 Kenako mitengoyo inauza mtengo wa mpesa kuti, ‘Bwera kuno, ukhale mfumu yathu.’ 13 Poyankha mtengo wa mpesawo unati, ‘Kodi ndisiye vinyo wanga watsopano amene amasangalatsa Mulungu ndi anthu,+ n’kupita kuti ndizikagwedezeka pamwamba pa mitengo ina?’ 14 Pamapeto pake, mitengo ina yonse inauza kamtengo kaminga+ kuti, ‘Bwera kuno, ukhale mfumu yathu.’ 15 Pamenepo kamtengo kamingako kanauza mitengoyo kuti, ‘Ngati mukunenadi zoona kuti mukufuna kundidzoza kuti ndikhale mfumu, bwerani mubisale mumthunzi wanga.+ Koma ngati si choncho, moto+ utuluke mwa ine ndi kunyeketsa mikungudza+ ya ku Lebanoni.’+

16 “Tsopano kodi mwachita zimenezi m’choonadi komanso kuchokera pansi pa mtima, moti mwalonga Abimeleki ufumu?+ Ndipo kodi Yerubaala ndi nyumba yake mwamuchitira zinthu zabwino? Kodi mwamuchitira mogwirizana ndi zimene iye anachita, 17 poika moyo wake pangozi+ pamene anakumenyerani nkhondo+ kuti akulanditseni m’manja mwa Amidiyani?+ 18 Kodi inu mwaukira nyumba ya bambo anga lero kuti muphe ana ake+ aamuna 70+ pamwala umodzi, kuti muike Abimeleki, mwana wa kapolo wake wamkazi,+ kukhala mfumu+ yolamulira nzika za Sekemu chifukwa chakuti ndi m’bale wanu? 19 Ngati lero mwachitira zimenezi Yerubaala ndi a m’nyumba yake m’choonadi komanso kuchokera pansi pa mtima, sangalalani ndi Abimeleki ndipo nayenso asangalale nanu.+ 20 Koma ngati si choncho, moto+ utuluke mwa Abimeleki ndi kunyeketsa nzika za Sekemu ndi anthu a m’nyumba ya Milo,+ komanso moto+ utuluke mwa nzika za Sekemu ndi anthu a m’nyumba ya Milo ndi kunyeketsa Abimeleki.”+

21 Zitatero Yotamu+ anathawira ku Beere, ndipo anakhala kumeneko chifukwa cha Abimeleki m’bale wake.

22 Choncho, Abimeleki modzikuza anakhala ngati mfumu ya Isiraeli zaka zitatu.+ 23 Ndiyeno Mulungu analola kuti pakhale kusamvana+ pakati pa Abimeleki ndi nzika za Sekemu, moti nzika za Sekemu zinayamba kuchitira Abimeleki zachinyengo.+ 24 Mulungu analola zimenezi kuti chiwawa chimene anachitira ana aamuna 70 a Yerubaala chiwabwerere pamutu pawo,+ ndi kuti aike magazi a anawo pa Abimeleki m’bale wawo chifukwa ndiye anawapha.+ Analolanso zimenezi kuti chiwawacho chibwerere pamutu pa nzika za Sekemu, chifukwa zinalimbikitsa+ Abimeleki kuti aphe abale ake. 25 Choncho, nzika za Sekemu zinamuikira obisalira anthu pamwamba pa mapiri kuti amuvulaze, ndipo obisalira anthuwo anali kulanda katundu wa munthu aliyense wodutsa njira imeneyo. Patapita nthawi, Abimeleki anauzidwa zimenezi.

26 Kenako kunabwera Gaala+ mwana wa Ebedi pamodzi ndi abale ake. Iwo analowa mu Sekemu,+ ndipo nzika za mu Sekemu zinayamba kum’khulupirira.+ 27 Ndiyeno monga mwa masiku onse, iwo analowa m’munda n’kuyamba kukolola ndi kuponda mphesa za m’minda yawo ndi kuchita chikondwerero.+ Kenako analowa m’nyumba ya mulungu wawo,+ ndipo anadya ndi kumwa+ ndi kutemberera+ Abimeleki. 28 Pamenepo Gaala mwana wa Ebedi anati: “Abimeleki ndani,+ ndipo Sekemu ndani kuti tim’tumikire? Kodi iye si mwana wa Yerubaala,+ ndipo mtumiki wake si Zebuli?+ Ena nonsenu tumikirani ana a Hamori,+ bambo a Sekemu, koma ifeyo tim’tumikire chifukwa chiyani? 29 Haa! Anthu awa akanakhala m’manja mwanga,+ ndikanam’chotsa Abimeleki.” Ndiyeno anauza Abimeleki kuti: “Chulukitsa asilikali ako ndipo udzamenyane ndi ine.”+

30 Pamene Zebuli, kalonga wa mzindawo, anamva mawu a Gaala mwana wa Ebedi,+ anakwiya koopsa. 31 Choncho anachitira chinyengo Gaala ndi kutumiza mithenga kwa Abimeleki kuti: “Gaala mwana wa Ebedi pamodzi ndi abale ake alowa mu Sekemu+ ndipo akulimbikitsa anthu a mumzindawu kuti akuukireni. 32 Tsopano inu mudzuke usiku+ pamodzi ndi anthu anu, ndipo mukam’bisalire+ m’thengo. 33 Ndiyeno mawa mudzuke mwamsanga dzuwa likangotuluka, ndi kuthamangira mumzindawo. Ndipo iye ndi anthu amene ali nawo akatuluka kudzamenyana nanu, mum’chitire zimene mungathe kuti mum’gonjetse.”

34 Pamenepo Abimeleki ndi anthu onse amene anali naye anadzuka usiku ndi kubisalira Sekemu, atagawana m’magulu anayi. 35 Patapita nthawi, Gaala+ mwana wa Ebedi anatuluka ndi kuima pachipata cha mzinda. Ndiyeno Abimeleki ndi anthu amene anali naye anadzuka m’malo amene anam’bisalira. 36 Gaala ataona anthuwo, nthawi yomweyo anauza Zebuli kuti: “Taona, anthu akutsika kuchokera pamwamba pa mapiri.” Koma Zebuli anati: “Si anthu amenewo, ukuona zithunzithunzi za mapiri.”+

37 Zitatero, Gaala ananenanso kuti: “Taona, anthu akubwera chakuno kuchokera pakati pa dziko, ndipo gulu limodzi likubwera kudzera njira yodutsa ku mtengo waukulu wa Meyonenimu.”* 38 Pamenepo Zebuli anamuuza kuti: “Kodi waiwala mawu ako aja amene unanena+ kuti, ‘Abimeleki ndani, kuti timutumikire?’+ Kodi amenewa si anthu amene unawakana?+ Ndiyetu pita, ukamenyane nawo.”

39 Choncho Gaala anatsogolera nzika za Sekemu ndi kuyamba kumenyana ndi Abimeleki. 40 Pamenepo Abimeleki anathamangitsa Gaala, ndipo Gaala anathawa. Anthu ochuluka anaphedwa ndipo mitembo inali paliponse mpaka kukafika kuchipata cha mzinda.

41 Zitatero, Abimeleki anapitiriza kukhala ku Aruma, ndipo Zebuli+ anathamangitsa Gaala+ ndi abale ake kuti asakhalenso m’Sekemu.+ 42 Ndiyeno tsiku lotsatira anthu anayamba kupita kunja kwa mzinda, ndipo ena anauza Abimeleki+ za nkhani imeneyi. 43 Atamva zimenezi anatenga anthu ake ndi kuwagawa m’magulu atatu+ n’kubisalira anthuwo m’thengo. Poyang’ana, anaona anthu akutuluka mumzindawo, ndipo anawaukira n’kuwakantha. 44 Abimeleki ndi magulu amene anali nawo anathamanga kuti akaime pachipata cha mzinda, pamene magulu ena awiri anathamangira kwa anthu amene anali kunja kwa mzinda, ndipo anayamba kuwakantha.+ 45 Ndiyeno Abimeleki anamenyana ndi mzindawo tsiku lonse, n’kuulanda. Anapha anthu amene anali mumzindawo+ ndipo anaugwetsa+ n’kuthira mchere panthaka ya mzindawo.+

46 Nzika zonse za munsanja ya Sekemu zitamva nkhani imeneyi, nthawi yomweyo zinalowa m’chipinda chotetezeka cha m’nyumba ya Eli-beriti.*+ 47 Ndiyeno Abimeleki anauzidwa kuti nzika zonse za munsanja ya Sekemu zasonkhana pamodzi. 48 Zitatero Abimeleki anakwera phiri la Zalimoni+ pamodzi ndi anthu onse amene anali naye. Tsopano Abimeleki anatenga nkhwangwa m’manja mwake, n’kudula nthambi ya mtengo, ndipo nthambiyo anainyamula n’kuiika paphewa lake. Pamenepo anauza anthu amene anali naye kuti: “Zimene mwaona ine ndikuchita, muchitenso zomwezo mofulumira!”+ 49 Chotero anthu onsewo, aliyense wa iwo anadula nthambi yake ndi kutsatira Abimeleki. Kenako anatsamiritsa nthambizo pachipinda chotetezekacho n’kuchiyatsa moto, moti nawonso anthu onse okhala munsanja ya Sekemu, amuna ndi akazi pafupifupi 1,000, anafa.+

50 Tsopano Abimeleki anapita ku Tebezi+ kumene anamenyana ndi mzindawo n’kuulanda. 51 Popeza pakati pa mzindawo panali nsanja yolimba, amuna ndi akazi onse, nzika zonse za mzindawo, zinathawira munsanjayo. Atalowa mmenemo, anatseka chitseko ndi kukwera padenga la nsanjayo. 52 Pamenepo Abimeleki anapita kunsanjayo ndi kuyamba kumenyana ndi anthu amene anali mmenemo. Ndiyeno anayandikira khomo la nsanjayo kuti aitenthe ndi moto.+ 53 Zitatero, mkazi wina anagwetsera mwala wa mphero pamutu wa Abimeleki ndi kuuphwanya.+ 54 Msangamsanga Abimeleki anaitana mtumiki wake womunyamulira zida ndi kumuuza kuti: “Tenga lupanga lako undiphe,+ kuopera kuti anthu anganene za ine kuti, ‘Anaphedwa ndi mkazi.’” Nthawi yomweyo, mtumiki wakeyo anamubaya* ndi lupanga, ndipo anafa.+

55 Tsopano anthu a mu Isiraeli ataona kuti Abimeleki wafa, aliyense wa iwo anapita kwawo. 56 Chotero Mulungu anachititsa zoipa zimene Abimeleki anachitira bambo ake mwa kupha abale ake 70, kum’bwerera pamutu pake.+ 57 Ndipo zoipa zonse za amuna a m’Sekemu, Mulungu anachititsa kuti ziwabwerere pamutu pawo, kuti temberero+ la Yotamu+ mwana wa Yerubaala,+ liwagwere.+

10 Pambuyo pa Abimeleki, panabwera Tola, munthu wa fuko la Isakara, amene anapulumutsa+ Isiraeli. Iye anali kukhala ku Samiri m’dera lamapiri la Efuraimu,+ ndipo anali mwana wa Puwa, amene anali mwana wa Dodo. 2 Iye anaweruza Isiraeli zaka 23. Kenako anamwalira ndipo anaikidwa ku Samiri.

3 Pambuyo pa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi.+ Iye anaweruza Isiraeli zaka 22. 4 Iye anadzakhala ndi ana 30 aamuna amene anali kuyenda pa abulu 30,+ ndipo iwo anali ndi mizinda 30. Mizinda imeneyi ikutchedwabe kuti Havoti-yairi*+ kufikira lero, ndipo ili m’dziko la Giliyadi. 5 Kenako Yairi anamwalira ndipo anaikidwa ku Kamoni.

6 Zitatero, ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ zifaniziro za Asitoreti,+ milungu ya ku Siriya,+ milungu ya ku Sidoni,+ milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya ana a Amoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Motero iwo anasiya Yehova ndipo sanam’tumikire.+ 7 Pamenepo, mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Isiraeli,+ moti anawagulitsa+ kwa Afilisiti+ ndi kwa ana a Amoni.+ 8 Choncho, amenewa anazunza ndi kupondereza kwambiri ana a Isiraeli chaka chimenecho. Kwa zaka 18, anapondereza ana onse a Isiraeli amene anali kum’mawa kwa Yorodano, m’dziko la Aamori limene linali ku Giliyadi. 9 Ndipo ana a Amoni anali kuwoloka Yorodano kukamenyana ndi fuko la Yuda, la Benjamini, ndi la Efuraimu, moti Isiraeli anasautsika kwambiri.+ 10 Pamenepo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Iwo anati: “Takuchimwirani+ inu Mulungu wathu, chifukwa takusiyani ndipo tikutumikira Abaala.”+

11 Ndiyeno Yehova anauza ana a Isiraeli kuti: “Kodi Aiguputo,+ Aamori,+ ana a Amoni,+ Afilisiti,+ 12 Asidoni,+ Aamaleki+ ndi Amidiyani+ atakuponderezani,+ sindinakupulumutseni m’manja mwawo mutafuulira kwa ine? 13 Koma inu munandisiya+ n’kuyamba kutumikira milungu ina.+ N’chifukwa chake sindidzakupulumutsaninso.+ 14 Pitani, kapempheni thandizo kwa milungu+ imene mwasankhayo.+ Milungu imeneyo ndi imene ikupulumutseni pa nthawi ya nsautso yanu.” 15 Poyankha, ana a Isiraeli anauza Yehova kuti: “Tachimwa.+ Inuyo mutichite zilizonse zimene zingakukomereni m’maso mwanu.+ Koma chonde, ingotipulumutsani lero.”+ 16 Atatero, iwo anayamba kuchotsa milungu yonse yachilendo pakati pawo+ n’kuyamba kutumikira Yehova,+ moti mtima wake+ unagwidwa ndi chisoni chifukwa cha kuvutika kwa ana a Isiraeli.+

17 Patapita nthawi, ana a Amoni+ anasonkhanitsidwa pamodzi ndipo anamanga msasa wawo ku Giliyadi.+ Zitatero, ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi ndi kumanga msasa wawo ku Mizipa.+ 18 Ndiyeno anthu ndi akalonga a Giliyadi anayamba kufunsana kuti: “Ndani atitsogolere kukamenyana ndi ana a Amoni?+ Ameneyo akhale mtsogoleri wa anthu onse okhala m’Giliyadi.”+

11 Tsopano Yefita+ wa ku Giliyadi+ anakhala mwamuna wamphamvu ndi wolimba mtima.+ Mayi ake anali hule,+ ndipo bambo ake omubereka anali Giliyadi. 2 Mkazi wa Giliyadi anapitiriza kumuberekera ana aamuna. Anawo atakula, anathamangitsa Yefita ndi kumuuza kuti: “Iwe suyenera kulandira cholowa m’nyumba ya bambo athu,+ chifukwa ndiwe mwana wa mayi wina.” 3 Choncho Yefita anathawa chifukwa cha abale ake ndipo anakakhala m’dziko la Tobu.+ Kumeneko anthu osowa ntchito anali kusonkhana kwa Yefita ndi kupita naye limodzi kukaukira adani awo.+

4 Ndiyeno patapita nthawi, ana a Amoni anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+ 5 Ana a Amoni atayamba kumenyana ndi Aisiraeli,+ akulu a ku Giliyadi anapita mwamsanga kukatenga Yefita kudziko la Tobu.+ 6 Iwo anauza Yefita kuti: “Tiye ukakhale mtsogoleri wa gulu lathu lankhondo, ndipo tikamenyane ndi ana a Amoni.” 7 Koma Yefita anauza akulu+ a ku Giliyadiwo kuti: “Kodi si inu amene munadana nane ndi kundithamangitsa m’nyumba ya bambo anga?+ N’chifukwa chiyani tsopano mwabwera kwa ine pamene mwakumana ndi mavuto?”+ 8 Pamenepo akulu a ku Giliyadi anayankha Yefita kuti: “Eya, n’chifukwa chake tsopano tabwerera+ kwa iwe. Choncho upite nafe kukamenyana ndi ana a Amoni, ndipo ukhale mtsogoleri wa anthu onse okhala ku Giliyadi.”+ 9 Ndiyeno Yefita anauza akulu a ku Giliyadiwo kuti: “Ngati mukunditenga kuti tikamenyane ndi ana a Amoni, ndipo Yehova akakawapereka+ m’manja mwanga, ndidzakhala mtsogoleri wanu!” 10 Poyankha akulu a ku Giliyadi anauza Yefita kuti: “Yehova amve makambirano athuwa+ ndi kutiweruza ngati sitidzachita zogwirizana ndi mawu ako.”+ 11 Pamenepo Yefita anapita ndi akulu a ku Giliyadi, ndipo anthu anamuika kukhala mtsogoleri wawo komanso mtsogoleri wa gulu lankhondo.+ Ndiyeno Yefita ananena mawu ake onse pamaso pa Yehova+ ku Mizipa.+

12 Kenako Yefita anatumiza mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni+ kuti: “Ndili nanu chiyani inu,+ kuti mubwere kudzamenyana nane m’dziko langa?” 13 Ndiyeno mfumu ya ana a Amoni inauza amithenga a Yefita kuti: “N’chifukwa chakuti Aisiraeli analanda dziko langa atatuluka mu Iguputo.+ Analanda dzikoli kuyambira ku Arinoni+ mpaka ku Yaboki ndi kukafikanso ku Yorodano.+ Tsopano undibwezere dzikoli mwamtendere.” 14 Koma Yefita anatumizanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni 15 ndipo anaiuza kuti:

“Yefita wanena kuti, ‘Aisiraeli sanatenge dziko la Mowabu+ ndi dziko la ana a Amoni.+ 16 Chifukwa Aisiraeli atatuluka mu Iguputo anayenda kudutsa m’chipululu kukafika ku Nyanja Yofiira+ mpaka ku Kadesi.+ 17 Kenako anatumiza mithenga kwa mfumu ya Edomu+ kuti: “Tiloleni tidutse m’dziko lanu,” koma mfumu ya Edomu sinamvere. Anatumizanso mithenga kwa mfumu ya Mowabu,+ koma nayonso sinavomereze. Choncho Aisiraeli anapitiriza kukhala ku Kadesi.+ 18 Pamene anali kudutsa m’chipululu, anayenda molambalala dziko la Edomu+ ndi dziko la Mowabu, moti anadutsa chakum’mawa kwa dziko la Mowabu+ ndi kukamanga misasa m’chigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu,+ chifukwa Arinoni ndiye anali malire a Mowabu.+

19 “‘Kenako Aisiraeli anatumiza mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ya ku Hesiboni,+ kuti: “Tiloleni tidutse m’dziko lanu kupita kumalo athu.”+ 20 Koma Sihoni sanakhulupirire kuti Aisiraeli akufuna kungodutsa m’dziko lake. Choncho Sihoni anasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi ndi kumanga misasa ku Yahazi+ n’kuyamba kumenyana ndi Aisiraeliwo.+ 21 Pamenepo Yehova Mulungu wa Aisiraeli anapereka Sihoni ndi anthu ake onse m’manja mwa Aisiraeli. Choncho anawagonjetsa ndi kutenga dziko lonse la Aamori okhala kumeneko.+ 22 Motero anatenga chigawo cha Aamori kuchokera ku Arinoni kukafika ku Yaboki ndiponso kuchokera kuchipululu kukafika ku Yorodano.+

23 “‘Choncho ndi Yehova Mulungu wa Aisiraeli amene anagonjetsa Aamori pamaso pa anthu ake Aisiraeli,+ ndipo iwe ukufuna kuwagonjetsa. 24 Kodi aliyense amene mulungu wako Kemosi+ wakuchititsa kuti umugonjetse, si amene udzam’gonjetsa? Chotero aliyense amene Yehova Mulungu wathu wam’gonjetsa pamaso pathu ndi amenenso ife tidzam’gonjetsa.+ 25 Tsopano kodi iweyo wasiyana pati ndi Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu?+ Kodi iye anakwanitsa kulimbana ndi Isiraeli, kapena kuyesa kumenyana naye? 26 Pamene Aisiraeli anali kukhala ku Hesiboni ndi m’midzi yake yozungulira,+ ku Aroweli+ ndi m’midzi yake yozungulira ndi m’mizinda yonse ya m’gombe la Arinoni kwa zaka 300, n’chifukwa chiyani simunawalande mizindayo pa nthawi imeneyo?+ 27 Ndipotu ine sindinakuchimwire, koma iwe ukundilakwira pomenyana nane. Yehova amene ndi Woweruza,+ aweruze lero pakati pa ana a Isiraeli ndi ana a Amoni.’”

28 Koma mfumu ya ana a Amoni siinamvere mawu amene Yefita anaitumizira.+

29 Tsopano mzimu wa Yehova unabwera pa Yefita+ ndipo anadutsa m’dera la Giliyadi, m’dera la Manase, ndi m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi.+ Atadutsa m’dera la Mizipe wa ku Giliyadi anafika kwa ana a Amoni.

30 Ndiyeno Yefita analonjeza+ Yehova kuti: “Ngati mudzaperekadi ana a Amoni m’manja mwanga, 31 ine ndidzapereka kwa Yehova+ aliyense amene adzatuluka m’nyumba yanga kudzandichingamira pamene ndikubwera mwamtendere+ kuchokera kwa ana a Amoni. Ndidzam’pereka monga nsembe yopsereza.”+

32 Zitatero Yefita anapita kwa ana a Amoni kukamenyana nawo ndipo Yehova anawapereka m’manja mwake. 33 Iye anakantha ana a Amoni kuyambira ku Aroweli mpaka kukafika ku Miniti,+ mizinda 20. Anawakantha koopsa mpaka kukafika ku Abele-kerami. Choncho ana a Amoni anagonja pamaso pa ana a Isiraeli.

34 Kenako Yefita anabwerera kwawo ku Mizipa.+ Atafika kumeneko anaona mwana wake wamkazi akubwera kudzam’chingamira, akuimba maseche ndi kuvina.+ Iye anali mwana yekhayo amene anali naye. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35 Atangomuona, anayamba kung’amba zovala zake+ ndi kunena kuti: “Kalanga ine mwana wanga! Wandiweramitsa ndi chisoni ndipo ine ndikukupitikitsa. Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mawu anga.”+

36 Koma iye anati: “Bambo, ngati mwatsegula pakamwa panu pamaso pa Yehova, ndichitireni mogwirizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu,+ chifukwa Yehova wakugwirirani ntchito yobwezera adani anu, ana a Amoni.” 37 Ndiyeno anapitiriza kuuza bambo akewo kuti: “Lolani izi zichitike kwa ine: Mundilole ndichoke kwa miyezi iwiri, ine pamodzi ndi atsikana anzanga, ndipite kumapiri, kukalirira unamwali wanga.”+

38 Pamenepo Yefita anati: “Pita!” Choncho anamulola kupita kwa miyezi iwiri. Ndiyeno iye pamodzi ndi atsikana anzake anapita kumapiri, kukalirira unamwali wake. 39 Ndiyeno miyezi iwiri itatha anabwerera kwa bambo ake. Pamenepo bambo akewo anakwaniritsa lonjezo lawo pa iye.+ Ndipo mtsikanayo sanagonepo ndi mwamuna. Chotero mu Isiraeli munakhala chizolowezi chakuti, 40 chaka ndi chaka ana aakazi a mu Isiraeli anali kupita kukayamikira mwana wamkazi wa Yefita wa ku Giliyadi, maulendo anayi pa chaka.+

12 Ndiyeno amuna a ku Efuraimu anasonkhana pamodzi n’kuwolokera tsidya lina chakumpoto, ndi kuuza Yefita kuti: “N’chifukwa chiyani unawoloka kukamenya ndi ana a Amoni ife osatiitana kuti tipite nawe?+ Tikutentha ndi moto pamodzi ndi nyumba yako.”+ 2 Koma Yefita anawauza kuti: “Ineyo ndi anthu anga tinalimbana koopsa ndi ana a Amoni.+ Inu ndinakuitanani kuti mudzandithandize koma simunandipulumutse m’manja mwawo. 3 Nditaona kuti inu simukubwera kudzandipulumutsa, ndinalolera kufa,* moti ndinapita kukamenyana ndi ana a Amoni,+ ndipo Yehova anawapereka m’manja mwanga.+ Tsopano n’chifukwa chiyani lero mwabwera kudzandiukira kuti mumenyane nane?”

4 Nthawi yomweyo Yefita anasonkhanitsa amuna onse a ku Giliyadi+ n’kumenyana ndi anthu a mu Efuraimu. Choncho amuna a ku Giliyadi anakantha Efuraimu, pakuti anati: “Ngakhale kuti inu anthu a mu Giliyadi mukukhala m’dera la Efuraimu ndi la Manase, kwenikweni ndinu gulu la anthu othawa ku Efuraimu.” 5 Ndiyeno amuna a ku Giliyadi anakatchinga powolokera Yorodano+ anthu a ku Efuraimu asanafike. Anthu othawa a ku Efuraimu akanena kuti: “Ndiloleni ndiwoloke,” pamenepo amuna a ku Giliyadi anali kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe wa ku Efuraimu?” Akayankha kuti: “Ayi!” 6 anali kumuuza kuti: “Nena kuti Shiboleti.”+ Koma iye anali kunena kuti: “Siboleti,” chifukwa sankatha kutchula mawuwa molondola. Akatero anali kumugwira ndi kumupha powolokera Yorodano pomwepo. Pa nthawi imeneyo panafa anthu 42,000 a ku Efuraimu.+

7 Yefita anaweruza Isiraeli zaka 6. Kenako Yefita wa ku Giliyadiyo anamwalira ndipo anaikidwa m’manda mumzinda wakwawo ku Giliyadi.

8 Pambuyo pa Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu+ anayamba kuweruza Isiraeli.+ 9 Ibizani anabereka ana aamuna 30 ndi ana aakazi 30. Iye anatuma anthu kukatenga atsikana 30 kuchokera kwina kuti akhale akazi a ana ake. Ndipo anaweruza Isiraeli kwa zaka 7. 10 Kenako Ibizani anamwalira ndipo anaikidwa m’manda ku Betelehemu.

11 Pambuyo pa Ibizani, Eloni wa fuko la Zebuloni+ anayamba kuweruza Isiraeli. Anaweruza Isiraeli zaka 10. 12 Kenako Eloni wa fuko la Zebuloni anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda ku Aijaloni m’dziko la Zebuloni.

13 Pambuyo pa Eloni, Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni,+ anayamba kuweruza Isiraeli. 14 Iye anabereka ana aamuna 40 ndipo anali ndi zidzukulu 30. Onsewa anali kuyenda pa abulu 70.+ Ndipo Abidoni anaweruza Isiraeli zaka 8. 15 Kenako Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda ku Piratoni, m’dziko la Efuraimu, m’phiri la Aamaleki.+

13 Tsopano ana a Isiraeli anayambiranso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ moti Yehova anawapereka m’manja mwa Afilisiti+ zaka 40.

2 Pa nthawiyi panali mwamuna wina wa ku Zora+ wa fuko la Dani,+ ndipo dzina lake anali Manowa.+ Mkazi wake anali wosabereka, moti analibe mwana.+ 3 Ndiyeno tsiku lina, mngelo wa Yehova anaonekera kwa mkaziyo+ ndi kumuuza kuti: “Tamvera, panopa ndiwe wosabereka ndipo ulibe mwana. Koma udzatenga pakati ndi kubereka mwana wamwamuna.+ 4 Choncho samala, usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa,+ ndipo usadye chilichonse chodetsedwa.+ 5 Pakuti udzatenga pakati ndi kubereka mwana wamwamuna. M’mutu mwake musadzadutse lezala+ chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri+ wa Mulungu potuluka m’mimba.+ Iye adzakhala patsogolo populumutsa Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.”+

6 Kenako mkaziyo anapita kukauza mwamuna wake kuti: “Munthu wa Mulungu woona anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ofanana ndi mngelo wa Mulungu woona,+ maonekedwe ochititsa mantha kwambiri.+ Koma sindinam’funse kumene wachokera ndiponso sanandiuze dzina lake.+ 7 Koma iye wandiuza kuti, ‘Pakuti udzakhala ndi pakati ndi kubereka mwana wamwamuna.+ Choncho, usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, ndipo usadye chilichonse chodetsedwa, chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri wa Mulungu potuluka m’mimba mpaka pa tsiku la imfa yake.’”+

8 Pamenepo Manowa anayamba kuchonderera Yehova kuti: “Yehova,+ lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwerenso kuti adzatilangize+ zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.”+ 9 Mulungu woona anamvetsera mawu a Manowa,+ moti mngelo wa Mulungu woona uja anabweranso kwa mkaziyo, ndipo anam’peza atakhala pansi kunja kwa mzinda. Pa nthawiyi sanali limodzi ndi mwamuna wake Manowa. 10 Nthawi yomweyo mkaziyo ananyamuka mofulumira ndi kuthamanga kukauza mwamuna wake+ kuti: “Munthu amene anabwera tsiku lija waonekeranso kwa ine.”+

11 Atatero, Manowa ananyamuka ndi kupitira limodzi ndi mkazi wakeyo kwa munthuyo ndipo anam’funsa kuti: “Kodi ndiwe amene unalankhula ndi mkazi uyu?”+ Poyankha iye anati: “Inde ndine.” 12 Ndiyeno Manowa anati: “Mawu ako akwaniritsidwe. Koma kodi mwanayo tidzamulere bwanji, nanga ntchito yake idzakhala yotani?”+ 13 Pamenepo mngelo wa Yehova anauza Manowa kuti: “Mkaziyu apewe kuchita zonse zimene ndamuletsa.+ 14 Asadye chilichonse chochokera ku mphesa zopangira vinyo, asamwe vinyo+ kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, ndipo asadye chilichonse chodetsedwa.+ Asunge zonse zimene ndamuuza.”+

15 Tsopano Manowa anauza mngelo wa Yehova kuti: “Tiloleni tikuchedwetseni pang’ono, kuti tikukonzereni kamwana ka mbuzi.”+ 16 Poyankha, mngelo wa Yehova anauza Manowa kuti: “Ngakhale mundichedwetse sindidya mkate wanu. Koma ngati mungathe kupereka kwa Yehova nsembe yopsereza,+ perekani.” Manowa ananena zimenezi chifukwa sanadziwe kuti anali mngelo wa Yehova. 17 Ndiyeno Manowa anafunsa mngelo wa Yehova kuti: “Dzina lanu ndani?+ Tikufuna tidzakulemekezeni mawu anu akadzakwaniritsidwa.” 18 Koma mngelo wa Yehovayo anamuyankha kuti: “Usandifunse dzina langa, chifukwa dzina langa ndi lodabwitsa.”

19 Pamenepo Manowa anatenga kamwana ka mbuzi ndi nsembe yambewu n’kuzipereka nsembe kwa Yehova pathanthwe.+ Ndipo Mulungu anali kuchita zodabwitsa, Manowa ndi mkazi wake akuonerera. 20 Pamene lawi la moto linali kukwera m’mwamba kuchokera paguwalo, mngelo wa Yehova nayenso anakwera kumwamba m’lawi la moto wa paguwa lansembelo, Manowa ndi mkazi wake akuonerera.+ Nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 21 Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Pamenepo Manowa anadziwa kuti anali mngelo wa Yehova.+ 22 Ndiyeno Manowa anauza mkazi wake kuti: “Ife tifa basi,+ chifukwa taona Mulungu.”+ 23 Koma mkazi wakeyo anati: “Yehova akanakhala kuti akufuna kutipha, sakanalandira m’manja mwathu nsembe yopsereza ndi nsembe yathu yambewu.+ Komanso sakanationetsa ndi kutiuza zinthu zonsezi.”+

24 Patapita nthawi, mkaziyo anabereka mwana wamwamuna ndipo dzina lake anamutcha kuti Samisoni.+ Mnyamatayo anali kukula, ndipo Yehova anapitiriza kumudalitsa.+ 25 Kenako mzimu wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa iye ku Mahane-dani+ pakati pa Zora+ ndi Esitaoli.+

14 Tsopano Samisoni anapita ku Timuna+ ndipo kumeneko anaona mkazi mwa ana aakazi a Afilisiti. 2 Kenako anapita kukauza bambo ndi mayi ake kuti: “Ine ndaona mkazi ku Timuna mwa ana aakazi a Afilisiti, choncho mukam’tenge kuti akhale mkazi wanga.”+ 3 Koma bambo ndi mayi akewo anam’funsa kuti: “Kodi wasowa mkazi pakati pa ana aakazi a abale ako ndi anthu onse a mtundu wathu,+ kuti upite kukatenga mkazi kwa Afilisiti osadulidwa?”+ Koma Samisoni anauza atate akewo kuti: “Ingonditengerani mkazi ameneyu, chifukwa ndi amene ali woyenera kwa ine?” 4 Bambo ndi mayi a Samisoni sanadziwe kuti Yehova ndi amene anali kuchititsa zimenezi.+ Iwo sanadziwe kuti anali kufunafuna mpata woti amenyane ndi Afilisiti, chifukwa pa nthawiyi Afilisiti anali kulamulira Isiraeli.+

5 Pamenepo Samisoni anapita ku Timuna+ pamodzi ndi bambo ndi mayi ake. Atafika m’minda ya mpesa ya ku Timuna, anakumana ndi mkango wamphamvu umene unayamba kubangula utamuona. 6 Ndiyeno mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye,+ moti anakhadzula mkangowo pakati ngati mmene munthu angakhadzulire kamwana ka mbuzi. Iye analibe chida chilichonse m’manja mwake. Zimene anachitazi sanauze bambo kapena mayi ake. 7 Iye anapita kwawo kwa mkazi uja ndipo analankhula naye. Kwa Samisoni, mkaziyu anali woyenerabe.+

8 Patapita nthawi, Samisoni anabwerera kwa mkaziyo kuti akam’tenge ndi kupita naye kwawo.+ Ali m’njira, anapatuka kuti aone mkango umene anapha uja. Atafika pamene anaphera mkango paja anapeza kuti m’thupi la mkango wakufa uja muli njuchi ndi uchi.+ 9 Ndiyeno anatengako uchiwo m’manja n’kumadya akuyenda.+ Atapezananso ndi bambo ndi mayi ake, anawagawira uchiwo ndipo iwo anayamba kudya. Iye sanawauze kuti uchiwo wautenga m’thupi la mkango wakufa.

10 Bambo ake anapitiriza ulendo wopita kwawo kwa mkazi uja, ndipo Samisoni anakonza phwando kumeneko,+ popeza umu ndi mmene achinyamata anali kuchitira. 11 Ndiyeno anthu a kumeneko atamuona, nthawi yomweyo anatenga amuna 30 kuti azikhala ndi Samisoni monga anzake a mkwati. 12 Kenako Samisoni anawauza kuti: “Ndiloleni ndikuphereni mwambi.+ Ngati mundiuza tanthauzo lake, m’masiku 7+ a phwandoli, ndidzakupatsani malaya 30 amkati ndi zovala zina 30.+ 13 Koma mukalephera kundiuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa malaya 30 amkati ndi zovala zina 30.” Atatero iwo anamuuza kuti: “Ipha mwambi wakowo kuti tiumve.” 14 Choncho iye anati:

“M’chinthu chodya zinzake+ munatuluka chakudya,

Ndipo m’chinthu champhamvu munatuluka zinthu zokoma.”+

Koma anzake a mkwatiwo analephera kumasulira mwambiwo kwa masiku atatu. 15 Ndiyeno pa tsiku lachinayi anayamba kuuza mkazi wa Samisoni kuti: “Umunyengerere mwamuna wako kuti atiuze tanthauzo la mwambiwu.+ Akapanda kutiuza, tikutentha ndi moto pamodzi ndi nyumba ya bambo ako.+ Kodi anthu inu mwatiitana kuti mutilande katundu wathu?”+ 16 Pamenepo mkazi wa Samisoni anayamba kulira pamaso pa mwamuna wake,+ ndipo ankamuuza kuti: “Umandida, sundikonda ayi.+ Iwe waphera mwambi anthu a mtundu wanga,+ koma ine sunandiuze tanthauzo lake.” Atatero anamuuza kuti: “Ndikuuze chifukwa chiyani, pamene bambo kapena mayi anga sindinawauze?”+ 17 Koma mkaziyo anapitiriza kulira pamaso pa Samisoni kwa masiku 7 a phwandolo. Pamapeto pake, pa tsiku la 7, Samisoni anauza mkaziyo tanthauzo lake chifukwa anamuumiriza.+ Kenako mkaziyo anaulula tanthauzo la mwambiwo kwa anthu a mtundu wake.+ 18 Choncho pa tsiku la 7, Samisoni asanalowe m’chipinda cha mkaziyo,+ amuna a mumzindawo anamuuza kuti:

“Kodi chokoma kuposa uchi n’chiyani,

Ndipo champhamvu kuposa mkango n’chiyani?”+

Poyankha iye anawauza kuti:

“Mukanapanda kulima ndi ng’ombe yanga yaikazi,+

Simukanatha kumasulira mwambi wanga.”+

19 Pamenepo mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye.+ Choncho anapita ku Asikeloni+ kumene anakapha amuna 30, ndipo anatenga zovala zawo n’kuzipereka kwa amene anamasulira mwambi aja.+ Koma mkwiyo wake unapitiriza kuyaka, ndipo anapita kunyumba ya bambo ake.

20 Koma mkazi wa Samisoni+ anakwatiwa ndi mwamuna amene anali kukhala ndi Samisoni,+ monga mnzake wa mkwati.

15 Ndiyeno patapita nthawi, m’masiku okolola tirigu, Samisoni anapita kukaona mkazi wake uja, atatenga kamwana ka mbuzi.+ Pamenepo iye anati: “Ndilowa m’chipinda cha mkazi wanga.”+ Koma bambo a mkaziyo sanam’lole kuti alowe. 2 Iwo anati: “Ine ndinali kuganiza kuti, ndithu ukudana naye mkaziyu,+ moti ndam’pereka kwa mwamuna amene anali kukhala nawe ngati mnzake wa mkwati.+ Kodi mng’ono wake wa mtsikanayu si wabwino kuposa iye? Bwanji osatenga ameneyu kukhala mkazi wako m’malo mwa iye?” 3 Koma Samisoni anawauza kuti: “Ulendo uno ndilibe mlandu ndi Afilisiti ngati ndingachite zinthu zowavulaza.”+

4 Pamenepo Samisoni ananyamuka ndi kugwira nkhandwe 300,+ ndipo anatenga nkhandwezo ziwiriziwiri n’kuzimanga michira. Atatero, anaika muuni umodzi pakati penipeni pa michira iwiriyo. 5 Kenako anayatsa miyuniyo ndi moto, n’kutumiza nkhandwezo m’minda ya Afilisti ya mbewu zosakolola. Choncho anayatsa chilichonse, kuyambira mitolo ya mbewu, mbewu zosakolola, minda ya mpesa mpaka minda ya maolivi.+

6 Zitatero, Afilisiti anayamba kufunsa kuti: “Wachita zimenezi ndani?” Ndiyeno iwo anati: “Ndi Samisoni, mkamwini wa munthu wa ku Timuna uja, chifukwa chakuti anatenga mkazi wake ndi kum’pereka kwa mwamuna amene anali mnzake wa mkwati.”+ Choncho Afilisiti anapita kukatentha ndi moto mtsikanayo pamodzi ndi bambo ake.+ 7 Pamenepo Samisoni anawauza kuti: “Pa zimene mwachitazi, ine sindingachitire mwina koma kukubwezerani,+ ndipo ndikatero ndisiyira pamenepo.” 8 Ndiyeno anayamba kuwakantha koopsa.* Kenako anayamba kukhala m’phanga la m’thanthwe la Etami.+

9 Patapita nthawi, Afilisiti+ anabwera ndi kumanga msasa ku Yuda,+ n’kuyamba kuyendayenda ku Lehi.+ 10 Pamenepo anthu a ku Yuda anati: “N’chifukwa chiyani mwabwera kudzatiukira?” Poyankha, iwo anati: “Tabwera kudzamanga Samisoni, kuti tim’chitire zimene iye watichitira.” 11 Zitatero, amuna 3,000 a ku Yuda anapita kuphanga la thanthwe la Etami+ ndi kuuza Samisoni kuti: “Kodi iwe, sukudziwa kuti Afilisiti ndi amene akutilamulira?+ Ndiye wachitiranji zimenezi kwa ife?” Iye anawayankha kuti: “Ndawachitira zimene iwo anandichitira.”+ 12 Koma iwo anamuuza kuti: “Ife tabwera kudzakumanga kuti tikupereke m’manja mwa Afilisiti.” Poyankha Samisoni anati: “Lumbirani kuti inuyo simundiukira.” 13 Iwo anamuyankha kuti: “Ayi, ife sitikupha. Tingokumanga ndi kukupereka m’manja mwawo.”

Pamenepo anam’manga ndi zingwe ziwiri zatsopano+ ndi kum’tulutsa kuphangako. 14 Choncho iye anafika ku Lehi, ndipo Afilisiti atamuona anafuula mokondwera.+ Pamenepo, mzimu wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa iye, ndipo zingwe zimene anam’manga nazo manja zija zinaduka ngati ulusi wowauka ndi moto,+ moti zinadukaduka ndi kugwa. 15 Zitatero, anapeza fupa laliwisi la nsagwada za bulu wamphongo, n’kukantha nalo amuna 1,000.+ 16 Pamenepo Samisoni anati:

“Ndi fupa la nsagwada za bulu wamphongo—milumilu!

Ndi fupa la nsagwada za bulu wamphongo, ndapha anthu 1,000.”+

17 Atamaliza kulankhula zimenezi, nthawi yomweyo anataya fupa lija ndi kutcha malowo kuti Ramati-lehi.*+ 18 Ndiyeno anamva ludzu koopsa, ndipo anayamba kufuulira Yehova kuti: “Ndinu amene mwapereka chipulumutso chachikulu chimenechi m’manja mwa mtumiki wanu.+ Tsopano kodi ndife ndi ludzu, ndigwere m’manja mwa anthu osadulidwa?”+ 19 Chotero Mulungu anang’amba nthaka ku Lehi ndipo madzi+ anayamba kutuluka panthakapo. Pamenepo Samisoni anamwa madziwo, moti anapezanso mphamvu+ ndi kutsitsimulidwa.+ N’chifukwa chake anatcha malowo kuti Eni-hakore.* Malo amenewa ali ku Lehi kufikira lero.

20 Chotero Samisoni anaweruza Isiraeli zaka 20 m’masiku a Afilisiti.+

16 Nthawi ina, Samisoni anapita ku Gaza+ ndipo anaona hule kumeneko ndi kulowa m’nyumba ya huleyo.+ 2 Pamenepo anthu a ku Gaza anauzidwa kuti: “Samisoni wabwera, ali kuno.” Choncho anam’zungulira+ ndi kum’bisalira usiku wonse kuchipata cha mzindawo.+ Iwo anakhala chete usiku wonse, n’kumanena mumtima mwawo kuti: “Kukangocha timuphe.”+

3 Koma Samisoni anagonabe mpaka pakati pa usiku. Kenako anadzuka pakati pa usikupo ndi kugwira zitseko za chipata cha mzinda+ pamodzi ndi nsanamira zake ziwiri, n’kuzizula pamodzi ndi mpiringidzo wake. Atatero anazinyamula pamapewa+ n’kupita nazo pamwamba pa phiri limene lili moyang’anana ndi Heburoni.+

4 Pambuyo pake, Samisoni anayamba kukonda mkazi wina kuchigwa* cha Soreki, ndipo dzina lake anali Delila.+ 5 Pamenepo olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anafika kwa mkaziyo ndi kumuuza kuti: “Umunyengerere+ kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zazikuluzo ndi zimene tingachite kuti timugonjetse. Ufufuzenso zimene tingam’mange nazo kuti tithane naye. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva zokwana 1,100.”+

6 Kenako Delila anauza Samisoni kuti: “Tandiuza, kodi chinsinsi cha mphamvu zako zazikuluzi n’chiyani? Ndipo kodi munthu angakumange ndi chiyani kuti athane nawe?”+ 7 Samisoni anamuyankha kuti: “Atandimanga ndi zingwe zatsopano zaziwisi 7 za mitsempha ya nyama,+ ndingafooke ndi kukhala ngati munthu wamba.” 8 Choncho olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anam’bweretsera zingwe zatsopano zaziwisi 7 za mitsempha ya nyama. Kenako Delila anamanga nazo Samisoni. 9 Pamenepa n’kuti anthu atabisalira Samisoni m’chipinda cha mkaziyo,+ ndipo mkaziyo anamuuza kuti: “Afilisiti+ aja abwera Samisoni!” Pamenepo Samisoni anadula zingwe zija pakati, monga mmene ulusi wopota wabwazi umadukira ukayandikira moto.+ Ndipo chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike.+

10 Kenako Delila+ anauza Samisoni kuti: “Iwe wandipusitsa pondiuza bodza.+ Tsopano ndiuze, chonde, zimene angakumange nazo.” 11 Poyankha Samisoni anamuuza kuti: “Atandimanga mwamphamvu ndi zingwe zatsopano zimene sanazigwiritsepo ntchito, ndingafooke ndi kukhala ngati munthu wamba.” 12 Ndiyeno Delila anatenga zingwe zatsopano ndi kum’manga nazo, n’kumuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Pa nthawiyi n’kuti anthu atam’bisalira m’chipinda cha mkaziyo.+ Pamenepo, Samisoni anadula pakati zingwe zimene anam’manga nazo manjazo, ngati kuti akudula ulusi.+

13 Kenako Delila anauza Samisoni kuti: “Wakhala ukundipusitsa mpaka pano mwa kundiuza bodza.+ Ndiuze zimene angakumange nazo.”+ Poyankha Samisoni anati: “Uluke zingongo 7 za m’mutu mwanga ndi ulusi wa m’litali+ mwa nsalu.” 14 Iye analukadi mwamphamvu zingongozo, n’kuzilimbitsa ndi chikhomo. Kenako anamuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!”+ Pamenepo Samisoni anagalamuka ku tulo take ndi kuzula chikhomo chija n’kudula ulusiwo.

15 Ndiyeno Delila anauza Samisoni kuti: “Kodi ulibe manyazi kundiuza kuti, ‘Ndimakukonda,’+ pamene mtima wako suli pa ine? Katatu konse tsopano wakhala ukundipusitsa, ndipo sunandiuze chinsinsi cha mphamvu zako zazikuluzi.”+ 16 Ndiyeno chifukwa chakuti Delila anapanikiza+ Samisoni ndi mawu ake mosalekeza, ndi kum’chonderera, Samisoni anafika potopa nazo kwambiri.+ 17 Pamapeto pake, Samisoni anamuululira zonse za pansi pa mtima wake,+ kuti: “M’mutu mwanga simunadutsepo lezala,+ chifukwa ndine Mnaziri wa Mulungu kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga.+ Atandimeta, mphamvu zanga zikhoza kundichokera, ndipo ndingafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.”+

18 Delila ataona kuti Samisoni wamuululira zonse za pansi pa mtima wake, nthawi yomweyo anatumiza mthenga kukaitana olamulira ogwirizana a Afilisiti,+ kuti: “Bwerani tsopano popeza wandiululira zonse za pansi pa mtima wake.”+ Pamenepo olamulira ogwirizana a Afilisiti aja anabwera kwa Delila ndipo anam’patsa ndalama.+ 19 Zitatero, Delila anagonetsa Samisoni tulo pamawondo ake, ndipo anaitana mwamuna wina amene anam’meta zingongo 7 za m’mutu mwake. Kenako Delila anayamba kukula mphamvu pa Samisoni ndipo mphamvu za Samisoni zinam’chokera. 20 Ndiyeno Delila anati: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Pamenepo Samisoni anagalamuka ku tulo take ndi kunena kuti: “Ndituluka monga mwa masiku onse+ kukalimbana nawo.” Koma iye sanadziwe kuti Yehova anali atam’chokera.+ 21 Chotero Afilisiti anam’gwira ndi kum’boola maso+ n’kupita naye ku Gaza.+ Anam’manga ndi zomangira ziwiri zamkuwa,+ ndipo anakhala woyendetsa mwala wa mphero+ m’ndende.+ 22 Atangometedwa, tsitsi lake linayamba kukula kwambiri.+

23 Ndiyeno olamulira ogwirizana a Afilisiti anasonkhana pamodzi kuti achite phwando lalikulu lopereka nsembe kwa Dagoni+ mulungu wawo, ndi kuchita chikondwerero, ndipo anali kunena kuti: “Mulungu wathu wapereka m’manja mwathu mdani wathu Samisoni!”+ 24 Anthu ataona Samisoni, nthawi yomweyo anayamba kutamanda mulungu wawo,+ kuti: “Mulungu wathu wapereka m’manja mwathu mdani wathu,+ ndi munthu wowononga dziko lathu,+ ndiponso amene anali kuchulukitsa chiwerengero cha anthu athu ophedwa.”+

25 Ndiyeno chifukwa chakuti mitima yawo inali yosangalala,+ anayamba kunena kuti: “Itanani Samisoni kuti adzatisangalatse.”+ Chotero anaitana Samisoni ndipo anam’tulutsa m’ndende kuti awachitire masewera.+ Atabwera anamuimiritsa pakati pa zipilala. 26 Pamenepo Samisoni anauza mnyamata amene anam’gwira dzanja kuti: “Ndilole ndigwire zipilala zimene zalimbitsa nyumbayi kuti ndizitsamire.” 27 (Pa nthawiyi m’nyumbamo munadzaza amuna ndi akazi, ndipo olamulira onse ogwirizana a Afilisiti anali mmenemo.+ Padenga la nyumbayo panali amuna ndi akazi pafupifupi 3,000 amene anali kuonerera Samisoni akuchita zoseketsa.)+

28 Ndiyeno Samisoni+ anafuulira Yehova,+ kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, chonde, ndikumbukireni+ ndi kundipatsa mphamvu+ kamodzi kokhaka, inu Mulungu woona. Ndiloleni ndiwabwezere Afilisiti chifukwa cha limodzi mwa maso anga awiriwa.”+

29 Pamenepo Samisoni anagwira mwamphamvu zipilala ziwiri zapakati zimene zinalimbitsa nyumbayo. Anagwira mwamphamvu chipilala chimodzi ndi dzanja lamanja ndipo chipilala china anachigwira ndi dzanja lamanzere. 30 Ndipo Samisoni anati: “Ndife nawo limodzi+ Afilisitiwa.” Pamenepo anawerama atasonkhanitsa mphamvu zake zonse moti nyumbayo inagwera olamulira ogwirizana a Afilisiti ndi anthu onse amene anali m’nyumbayo.+ Anthu amene Samisoni anawapha pa imfa yake anali ambiri kuposa anthu amene anawapha pa moyo wake.+

31 Kenako abale ake ndi anthu onse a m’nyumba ya bambo ake, anapita kumeneko kukatenga mtembo wa Samisoni ndi kubwera nawo kwawo, ndipo anamuika m’manda a bambo ake Manowa,+ pakati pa Zora+ ndi Esitaoli.+ Samisoni anali ataweruza Isiraeli zaka 20.+

17 Panali mwamuna wina wa kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Mika. 2 Nthawi ina anauza mayi ake kuti: “Ndalama zanu zasiliva zokwana 1,100 zimene zinasowa zija, zimene munatemberera+ nazo munthu amene anazibayo, ine ndikumva, zili ndi ine. Ndine amene ndinatenga.”+ Pamenepo mayi akewo anati: “Yehova akudalitse mwana wanga.”+ 3 Ndiyeno anabweza ndalama zasiliva zokwana 1,100 zija kwa mayi ake.+ Atabweza ndalamazo, mayi akewo anati: “Ndithudi ndipereka ndalama zasilivazi kwa Yehova kuti zikhale zopatulika. Ndichita zimenezi kuti ndithandize mwana wanga, ndi kuti papangidwe chifaniziro chosema+ ndiponso chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Tsopano ndikubweza ndalamazi kwa iwe.”

4 Koma Mika anabweza ndalamazo kwa mayi ake, ndipo mayi akewo anatenga ndalama zasiliva zokwana 200 n’kuzipereka kwa wosula siliva.+ Pamenepo wosula silivayo anapanga chifaniziro chosema+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Zinthu zimenezi anaziika m’nyumba ya Mika. 5 Ndiyeno Mika anali ndi nyumba ya milungu,+ chotero anapanga efodi+ ndi aterafi,*+ komanso anapatsa mmodzi mwa ana ake mphamvu,*+ kuti azitumikira monga wansembe wake.+ 6 Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Aliyense anali kuchita zimene anali kuona kuti n’zoyenera.+

7 Ndiyeno mu Betelehemu+ wa ku Yuda munali mnyamata wina, wa m’banja la Yuda, ndipo anali Mlevi.+ Iye anakhala kumeneko kwa kanthawi. 8 Mnyamata ameneyu anachoka kumzinda wa Betelehemu wa ku Yuda, kuti akakhale kwa kanthawi kulikonse kumene angapeze malo okhala. Atayenda mtunda wautali ndithu, anafika m’dera lamapiri la Efuraimu, mpaka kunyumba ya Mika.+ 9 Pamenepo Mika anam’funsa kuti: “Wachokera kuti?” Poyankha, iye anati: “Ine ndine Mlevi. Ndachokera ku Betelehemu wa ku Yuda, ndipo ndikupita kulikonse kumene ndingapeze malo okhala, kuti ndikakhale kumeneko kwa kanthawi.” 10 Atatero Mika anamuuza kuti: “Ukhale ndi ine ndipo uzitumikira ngati tate+ ndi wansembe+ wanga. Ine ndizikupatsa ndalama zasiliva 10 pa chaka, komanso zovala zako zoyenera ndi chakudya.” Pamenepo Mleviyo analowa m’nyumbamo. 11 Choncho Mleviyo anavomera kukhala ndi Mika ndipo anakhala ngati mmodzi wa ana a Mika. 12 Kuwonjezera apo, Mika anapatsa mphamvu Mleviyo+ kuti atumikire monga wansembe+ wake ndi kupitiriza kukhala m’nyumba ya Mika. 13 Choncho Mika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova andichitira zabwino, chifukwa Mlevi wakhala wansembe wanga.”+

18 Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndipo m’masiku amenewo fuko la Dani+ linali kufuna cholowa chake kuti likakhale kumeneko, chifukwa mpaka pa nthawi imeneyi linali lisanalandirebe cholowa pakati pa mafuko onse a Isiraeli.+

2 Nthawi ina, ana a Dani anatumiza amuna asanu a m’banja lawo, amuna olimba mtima ochokera pakati pawo, kuchokera kumizinda ya Zora+ ndi Esitaoli+ kuti akazonde dziko ndi kuliyendera. Ndiyeno anawauza kuti: “Pitani mukaone+ dzikolo.” Choncho anafika kudera lamapiri la Efuraimu,+ mpaka kunyumba ya Mika,+ ndipo anagona kumeneko. 3 Atayandikira nyumba ya Mika anamva ndi kuzindikira mawu a mnyamata uja, Mlevi. Motero anapatukira kumeneko ndi kum’funsa kuti: “Wabwera ndi ndani kuno ndipo ukudzachita chiyani? Chimene ukufuna kuno n’chiyani?” 4 Poyankha iye anati: “Mika anagwirizana ndi ine kuti andilembe ntchito,+ ndi cholinga choti ndizitumikira monga wansembe+ wake.” 5 Ndiyeno iwo anamuuza kuti: “Tifunsire+ kwa Mulungu+ kuti tidziwe ngati kumene tikupita tidzayendako bwino.” 6 Pamenepo wansembeyo anawauza kuti: “Pitani mu mtendere. Yehova ali ndi inu pa ulendowu.”

7 Choncho amuna asanu aja anapitiriza ulendo wawo ndipo anafika kumzinda wa Laisi.+ Kumeneko anaona kuti anthu a mumzindawo anali kukhala mosadalira aliyense, malinga ndi chikhalidwe cha Asidoni. Iwo anali kukhala phee, mosatekeseka,+ ndipo panalibe amene anawagonjetsa n’kumawachitira nkhanza kapena kuwavutitsa m’dzikolo. Kuwonjezera apo, anali kukhala kutali kwambiri ndi Asidoni+ ndipo sanali kuyenderana ndi anthu a m’madera ena.

8 Patapita nthawi, anafika kwa abale awo ku Zora+ ndi ku Esitaoli.+ Ndipo abale awo anayamba kuwafunsa kuti: “Munayendako bwanji?” 9 Poyankha iwo anati: “Nyamukani, tiyeni tipite kukamenyana nawo, chifukwa ife taliona dzikolo ndipo ndi labwino kwambiri.+ Mukuzengerezatu. Musachite ulesi, koma nyamukani mukatenge dzikolo kukhala lanu.+ 10 Mukakafika kumeneko, mukapeza anthu okhala mosatekeseka,+ ndipo dzikolo ndi lalikulu kwambiri. Mulungu walipereka m’manja mwanu,+ ndipo ndi dziko losasowa kena kalikonse kopezeka padziko lapansi.”+

11 Pamenepo amuna 600 ovala zida zankhondo, ochokera m’banja la Dani,+ ananyamuka ku Zora ndi ku Esitaoli.+ 12 Amunawa ananyamuka pa ulendo wawo ndipo anayenda mpaka kukafika pafupi ndi Kiriyati-yearimu+ ku Yuda, n’kumanga msasa pamenepo. N’chifukwa chake malowo amatchedwa dzina lakuti Mahane-dani*+ kufikira lero. Malo amenewa ali kumadzulo kwa Kiriyati-yearimu. 13 Atachoka pamenepo, anayenda ndi kukafika kudera lamapiri la Efuraimu, mpaka kukafika kunyumba ya Mika.+

14 Ndiyeno amuna asanu amene anapita kukazonda+ dziko la Laisi+ aja, anauza abale awo kuti: “Kodi mukudziwa kuti m’nyumba izi muli efodi, aterafi,+ chifaniziro chosema+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula?+ Ndiyetu dziwani chochita.”+ 15 Choncho anapatukira kumeneko ndi kufika panyumba ya mnyamata uja, Mlevi,+ kunyumba ya Mika. Pamenepo anayamba kulonjerana naye.+ 16 Pamenepa n’kuti amuna 600 ovala zida zankhondo aja,+ ana a Dani,+ ataima pachipata. 17 Tsopano amuna asanu amene anapita kukazonda dziko+ aja anapita kuti akalowe m’nyumba ndi kutenga chifaniziro chosema,+ efodi,+ aterafi+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ (Wansembe+ uja anali ataima pachipata pamodzi ndi amuna 600 ovala zida zankhondowo.) 18 Amuna asanuwo analowa m’nyumba ya Mika ndi kutenga chifaniziro chosema, efodi, aterafi ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Atatero wansembeyo+ anawafunsa kuti: “Mukutani kodi?” 19 Iwo anamuyankha kuti: “Khala chete. Gwira pakamwa pako, ndipo upite nafe kuti ukakhale tate+ ndi wansembe+ wathu. Chabwino n’chiti, kuti upitirize kukhala wansembe m’nyumba ya munthu mmodzi,+ kapena kuti ukhale wansembe wa banja ndi fuko lonse mu Isiraeli?”+ 20 Mtima wa wansembeyo unasangalala+ atamva mawu amenewa, ndipo iye anatenga efodi, aterafi ndi chifaniziro chosema+ n’kulowa pakati pa anthuwo.

21 Pamenepo anatembenuka n’kuyamba ulendo wawo, ndipo anaika patsogolo ana, ziweto ndi zinthu zamtengo wapatali.+ 22 Ndiyeno atayenda kamtunda ndithu kuchokera panyumba ya Mika, anthu a m’nyumba zoyandikana ndi nyumba ya Mika+ anasonkhanitsidwa pamodzi n’kuyamba kutsatira ana a Dani kuti apezane nawo. 23 Pamene anthuwo anali kufuulira ana a Dani, ana a Daniwo anatembenuka ndi kufunsa Mika kuti: “Vuto lako n’chiyani+ kuti usonkhanitse anthu onsewa?” 24 Poyankha, iye anati: “Mwatenga milungu yanga+ imene ndinapanga,+ ndipo mwatenganso wansembe+ n’kumapita naye. Nanga ine nditsala ndi chiyani?+ Ndiye mungandifunse bwanji kuti, ‘Vuto lako n’chiyani?’” 25 Pamenepo ana a Dani anamuuza kuti: “Usayandikire kuno ndipo tisamvenso mawu akowo, chifukwa anthu olusa+ angakupwetekeni, ndipo iweyo ungataye moyo wako ndi kutayitsa moyo wa anthu a m’nyumba yako.” 26 Zitatero ana a Dani anapitiriza ulendo wawo, ndipo Mika anaona kuti anali amphamvu kuposa iye.+ Chotero Mika anatembenuka ndi kubwerera kunyumba kwake.

27 Ana a Dani anatenga zimene Mika anapanga komanso wansembe+ wake, ndipo anapitiriza ulendo wawo wa ku Laisi+ kukaukira anthu aphee ndi osatekeseka.+ Atafika kumeneko anapha anthuwo ndi lupanga+ n’kutentha mzindawo ndi moto.+ 28 Iwo analibe owalanditsa chifukwa mzindawo unali kutali ndi Sidoni+ ndipo sankayenderana ndi anthu a m’madera ena. Komanso, mzindawo unali m’chigwa cha Beti-rehobu.+ Choncho ana a Dani anamanganso mzindawo ndi kuyamba kukhalamo.+ 29 Kuwonjezera apo, anatcha mzindawo kuti Dani, kutengera dzina la bambo awo lakuti Dani,+ amene anali wobadwa kwa Isiraeli.+ Ngakhale zili choncho, dzina loyamba la mzindawo linali Laisi.+ 30 Kenako ana a Dani anadziimikira chifaniziro chosema+ chija, ndipo Yonatani+ mwana wa Gerisomu,+ mwana wa Mose, pamodzi ndi ana ake, anakhala ansembe a fuko la Dani kufikira tsiku limene anthu a m’dzikolo anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+ 31 Ndipo chifaniziro chosema chimene Mika anapanga chinakhalabe choimiritsa masiku onse amene nyumba+ ya Mulungu woona inakhalabe ku Silo.+

19 Tsopano masiku amenewo, mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndiyeno Mlevi wina anakhala kwa kanthawi m’dera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu.+ Patapita nthawi, anatenga mkazi wa ku Betelehemu,+ ku Yuda, kukhala mdzakazi wake.+ 2 Mdzakazi wakeyo anakhala wosakhulupirika kwa iye, moti anayamba kuchita dama.+ Pamapeto pake, mkaziyo anachoka n’kukakhala kwa bambo ake ku Betelehemu wa ku Yuda miyezi inayi yathunthu. 3 Zitatero, mwamuna wakeyo ananyamuka kukakambirana naye mofatsa kuti abwerere. Pa ulendowo anali limodzi ndi mtumiki wake+ ndi abulu awiri. Atafika kumeneko, mkaziyo analowetsa mwamuna wakeyo m’nyumba ya bambo ake ndipo iwo atamuona anasangalala kwambiri kukumana naye. 4 Ndiyeno apongozi akewo, bambo a mtsikanayo, anam’chonderera kuti akhalebe, moti anakhala ndi kugona kumeneko masiku atatu. Masiku onsewa, iwo anali kudya ndi kumwa.+

5 Pa tsiku lachinayi, atadzuka m’mawa kwambiri monga mwa nthawi zonse, anakonzeka kuti anyamuke, koma bambo a mtsikanayo anauza mkamwini wawoyo kuti: “Yambani mwadya kaye mkate,+ kenako mukhoza kupita.” 6 Choncho anakhala pansi ndipo onse awiri anayamba kudya ndi kumwera pamodzi. Kenako bambo a mtsikanayo anauza mwamunayo kuti: “Chonde, lero mugone, mupite mawa,+ ndipo musangalatse mtima wanu.”+ 7 Mwamunayo ataimirira kuti azipita, apongozi ake anapitirizabe kum’chonderera, moti anagonanso komweko.+

8 Atadzuka m’mawa kwambiri tsiku lachisanu kuti azipita, bambo a mtsikanayo anati: “Idyaniko chakudya kuti musangalatse mtima wanu.”+ Pamenepo iwo anakhalabe mpaka chakumadzulo, ndipo onse awiri anali kudya. 9 Tsopano mwamunayo+ anaimirira kuti azipita, iyeyo pamodzi ndi mdzakazi wake+ ndiponso mtumiki wake,+ koma apongozi ake, bambo a mtsikanayo, anamuuza kuti: “Anotu ndi madzulo tsopano, ndipo posachedwa kuchita mdima. Chonde, lero mugone kuno.+ Onani, kunja kwatsala pang’ono kuda. Lero mugone kuno ndipo musangalatse mtima wanu.+ Mawa mudzuke m’mawa kwambiri ndi kuyamba ulendo wanu wopita kuhema wanu.” 10 Koma mwamunayo sanavomere kuti agone, ndipo ananyamuka ndi kuyamba ulendo wake. Iye anayenda mpaka kukafika pafupi ndi Yebusi,+ amene ndi Yerusalemu.+ Pa ulendowu, anali ndi abulu awiri amphongo aja, okhala ndi zishalo, ndipo analinso ndi mdzakazi wake ndi mtumiki wake.

11 Pamene ankayandikira Yebusi, dzuwa linali litapendeka ndithu,+ ndipo mtumiki uja anauza mbuye wake kuti: “Tiyeni tipatukire mumzinda uwu wa Ayebusi+ kuti tigone mmenemu.” 12 Poyankha mbuye wakeyo anati: “Tisapatukire mumzinda wa anthu achilendo+ amene si ana a Isiraeli. Tiyeni tipitirire ndi kukafika ku Gibeya.”+ 13 Anauzanso mtumiki wakeyo kuti: “Tiyeni tifike pa amodzi mwa malo awa, Gibeya kapena Rama,+ ndipo tigone kumeneko.” 14 Choncho anadutsa ndi kupitirizabe ulendo wawo ndipo dzuwa linayamba kulowa atayandikira Gibeya, m’dera la Benjamini.

15 Atafika kumzinda wa Gibeya, anapatuka kuti akalowe ndi kugona mmenemo. Ndiyeno analowa ndi kukhala pabwalo la mzindawo. Koma panalibe wowatenga kuti akagone m’nyumba yake.+ 16 Patapita nthawi, mwamuna wina wokalamba anatulukira madzulowo+ akuchokera ku ntchito yake ya kumunda. Kwawo kwa mwamunayo kunali kudera lamapiri la Efuraimu,+ ndipo anali kukhala ku Gibeya kwa kanthawi, koma amuna a mumzindawo anali Abenjamini.+ 17 Atakweza maso, anaona mwamuna wapaulendoyo ali m’bwalo la mzinda. Pamenepo mwamuna wokalambayo anam’funsa kuti: “Ukupita kuti, ndipo ukuchokera kuti?”+ 18 Poyankha anamuuza kuti: “Tikudutsa kuchokera ku Betelehemu wa ku Yuda kupita kudera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu.+ Kumeneko ndiye kwathu, koma ndinapita ku Betelehemu wa ku Yuda.+ Panopa ndikupita kunyumba kwanga, koma palibe amene akunditenga kuti ndikagone m’nyumba yake.+ 19 Udzu ndi chakudya+ china cha abulu athu tili nazo, ndipo tilinso ndi mkate+ ndi vinyo wa ine ndi kapolo wanu wamkazi+ komanso wa mtumiki+ wa kapolo wanu. Sitikusowa kanthu.” 20 Koma mwamuna wokalamba uja anati: “Mtendere ukhale nawe!+ Ine ndidzakupatsa chilichonse chimene ungafunikire.+ Koma usagone pabwalo la mzinda.” 21 Atatero anatengera Mlevi uja kunyumba kwake+ ndipo anapatsa abulu ake aja chakudya.+ Ndiyeno anasamba mapazi awo+ n’kuyamba kudya ndi kumwa.

22 Pamene anali kusangalatsa mitima yawo,+ mwadzidzidzi amuna a mumzindawo, anthu opanda pake,+ anazungulira nyumbayo,+ ndipo anali kukankhanakankhana pachitseko. Iwo anali kuuza mwamuna wokalamba uja, mwini nyumbayo, kuti: “Tulutsa mwamuna amene wabwera m’nyumba yako kuti tigone naye.”+ 23 Pamenepo mwini nyumbayo anatuluka ndi kuwauza kuti:+ “Iyayi abale anga,+ chonde, musachite choipa chilichonse, chifukwa munthuyu wabwera m’nyumba yanga. Musachite chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi ngati chimenechi.+ 24 Ndili ndi mwana wamkazi amene ndi namwali ndiponso pali mdzakazi wa mwamunayu. Ndiloleni ndiwatulutse, muwagwirire+ amenewa ndi kuchita nawo chilichonse chimene mungafune. Koma mwamunayu musam’chite chinthu chochititsa manyazi ndi chopusa ngati chimenechi.”

25 Koma amunawo sanafune kumumvera, moti Mleviyo anatenga mdzakazi wake+ ndi kum’pereka kwa amunawo kunja. Pamenepo, anthuwo anayamba kumugona,+ ndipo anapitiriza kum’zunza+ usiku wonse mpaka m’mawa. M’bandakucha anamusiya kuti apite. 26 Kutayamba kucha, mkaziyo anafika ndi kugwera pakhomo la nyumba ya mwamuna uja, mmene munali mbuye wake,+ ndipo anakhala pomwepo kufikira kutayera. 27 Mbuye wake anadzuka m’mawa ndi kutsegula zitseko za nyumbayo, n’kutuluka kuti ayambe ulendo wake. Mwadzidzidzi, anangopeza mkazi uja, mdzakazi wake,+ ali thapsa patsogolo pa nyumba, manja ake ali pakhomo la nyumbayo! 28 Ndiyeno anauza mkaziyo kuti: “Dzuka tizipita.” Koma sanamuyankhe.+ Zitatero, anamukweza pabulu n’kupita kunyumba kwake.+

29 Atafika kwawo, analowa m’nyumba yake ndi kutenga mpeni wophera nyama, n’kuduladula mdzakazi wake uja zigawo 12,+ n’kuzitumiza m’dera lililonse la Isiraeli.+ 30 Zitatero, aliyense amene anaona zimenezo anati: “Zoterezi sizinachitikepo kapena kuonekapo kuchokera pa tsiku limene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo mpaka lero. Iganizireni mofatsa nkhaniyi, munenepo maganizo+ anu ndipo tigwirizane.”

20 Chotero ana onse a Isiraeli anatuluka,+ kuchokera ku Dani+ mpaka kumunsi ku Beere-seba,+ ndipo khamu lonselo linasonkhana pamodzi mogwirizana+ kwa Yehova ku Mizipa,+ pamodzinso ndi anthu a m’dera la Giliyadi.+ 2 Zitatero, atsogoleri a anthu ndi mafuko onse a Isiraeli anaimirira pakati pa mpingo wonse wa anthu a Mulungu woona.+ Amuna ogwira lupanga oyenda pansi analipo 400,000.+

3 Ana a Benjamini anamva kuti ana a Isiraeli apita ku Mizipa.+

Pamenepo ana a Isiraeli anati: “Lankhulani, kodi chinthu choipachi chachitika bwanji?”+ 4 Poyankha, Mleviyo,+ mwamuna wa mkazi wophedwayo, anati: “Ine pamodzi ndi mdzakazi wanga,+ ndinafika ku Gibeya,+ m’dera la Benjamini, kuti ndigone kumeneko. 5 Ndiyeno anthu a m’Gibeya anayamba kundiukira, ndipo usiku anazungulira nyumba imene ndinalimo. Iwo anali kufuna kupha ineyo, koma anagwirira mdzakazi wanga+ mpaka anafa.+ 6 Choncho ndinatenga mdzakazi wanga ndi kum’duladula, n’kutumiza ziwalozo m’dera lililonse la cholowa cha Isiraeli.+ Ndinatero chifukwa iwo anachita khalidwe lotayirira+ komanso chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli.+ 7 Nkhani yaketu ndi imeneyi, inu nonse ana a Isiraeli. Nenanipo mawu anu ndi maganizo anu.”+

8 Pamenepo anthu onse ananyamuka mogwirizana,+ ndipo anati: “Aliyense wa ife sapitanso ku hema wake kapena kupatukira kunyumba yake.+ 9 Koma Gibeya tim’chitire izi: Tichite maere+ ndi kupita kukamenyana naye. 10 Ndipo m’mafuko onse a Isiraeli titengemo amuna 10 mwa amuna 100 alionse, amuna 100 mwa amuna 1,000 alionse, amuna 1,000 mwa amuna 10,000 alionse. Amenewa azipezera anthu zofunika, kuti anthuwo achitepo kanthu mwa kupita ndi kukamenyana ndi Gibeya wa ku Benjamini, chifukwa cha chinthu chochititsa manyazi ndi chopusa+ chimene achita mu Isiraeli.” 11 Chotero amuna onse a Isiraeli anasonkhana mogwirizana kuti amenyane ndi mzinda wa Gibeya, atapanga gulu limodzi lankhondo.

12 Ndiyeno mafuko a Isiraeli anatumiza amuna kwa atsogoleri onse a fuko la Benjamini,+ kuti: “Kodi chinthu choipachi chimene chachitika pakati panu n’chiyani?+ 13 Ndiyetu tipatseni amunawo,+ anthu opanda pakewo,+ amene ali mu Gibeya,+ kuti tiwaphe+ ndi kuchotsa choipachi mu Isiraeli.”+ Koma ana a Benjamini sanafune kumvera mawu a abale awo, ana a Isiraeli.+

14 Ndiyeno ana a Benjamini anasonkhana pamodzi ku Gibeya, kuchokera m’mizinda, kuti akamenyane ndi ana a Isiraeli. 15 Choncho ana a Benjamini anasonkhana pamodzi tsiku limenelo kuchokera m’mizinda. Iwo anali amuna ogwira lupanga okwanira 26,000,+ osawerengera anthu okhala m’Gibeya, mmene anasonkhanitsa amuna 700 osankhidwa mwapadera. 16 Pakati pa anthu onsewa, panali anthu amanzere+ 700 osankhidwa mwapadera. Aliyense wa anthu amenewa anali wamaluli poponya miyala*+ ndipo sanali kuphonya.

17 Amuna ogwira lupanga a mu Isiraeli amene anasonkhanitsidwa pamodzi anali 400,000,+ kupatulapo amuna a m’dera la Benjamini. Aliyense wa amenewa anali mwamuna wankhondo. 18 Ndipo ana a Isiraeli ananyamuka ndi kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu,+ kuti: “Ndani wa ife ayenera kutitsogolera kunkhondo yomenyana ndi ana a Benjamini?”+ Poyankha, Yehova anati: “Yuda akutsogolereni.”+

19 Zitatero, ana a Isiraeli ananyamuka m’mawa kwambiri ndi kukamanga msasa kuti amenyane ndi Gibeya.

20 Tsopano amuna a Isiraeli anapita kukamenyana ndi ana a Benjamini ku Gibeya, ndipo kumeneko amuna a Isiraeliwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo. 21 Zitatero, ana a Benjamini anatuluka m’Gibeya+ ndi kupha amuna a Isiraeli 22,000 tsiku limenelo, n’kusiya mitembo yawo itagonagona pansi.+ 22 Koma anthuwo, amuna a Isiraeli, analimba mtima ndipo anapitanso kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo pamalo omwe anafola tsiku loyamba lija. 23 Ndiyeno ana a Isiraeli anapita ku Beteli ndipo analira+ pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsira kwa Yehova, kuti: “Kodi ndipitenso kukamenyana ndi ana a m’bale wanga Benjamini?”+ Poyankha, Yehova anati: “Pita, kamenyane naye.”

24 Chotero ana a Isiraeli anapitanso kwa ana a Benjamini tsiku lachiwiri.+ 25 Pamenepo ana a Benjamini anatuluka m’Gibeya kudzakumana nawo tsiku lachiwirilo, ndipo anaphanso amuna ena 18,000 mwa ana a Isiraeli, n’kusiya mitembo yawo itagonagona pansi.+ Ophedwa onsewa anali amuna ogwira lupanga.+ 26 Zitatero, ana onse a Isiraeli,+ anthu onse, anapita mpaka anakafika ku Beteli. Kumeneko analira+ ndipo anakhala pansi pamaso pa Yehova ndi kusala kudya+ tsiku limenelo mpaka madzulo. Iwo anapereka nsembe zopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano+ kwa Yehova. 27 Kenako ana a Isiraeli anafunsira kwa Yehova,+ chifukwa masiku amenewo likasa la pangano+ la Mulungu woona linali ku Beteli komweko. 28 Masiku amenewo Pinihasi,+ mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye anali kuimirira pafupi ndi likasalo.+ Chotero iye anafunsa kuti: “Kodi ndipitenso kukamenyana ndi ana a m’bale wanga Benjamini kapena ndisapite?”+ Poyankha, Yehova anati: “Pita, chifukwa mawa ndim’pereka m’dzanja lako.”+ 29 Pamenepo Isiraeli anaika amuna kuti abisalire+ mzinda wonse wa Gibeya.

30 Chotero ana a Isiraeli anapita kwa ana a Benjamini tsiku lachitatu, n’kuyamba kufola mwa dongosolo lankhondo, kuti amenyane ndi Gibeya monga pa nthawi zina zoyamba zija.+ 31 Ana a Benjamini atatuluka kuti akakumane ndi anthuwo, anakokedwera kutali ndi mzinda.+ Ndiyeno monga mmene zinachitikira maulendo oyamba aja, ana a Benjaminiwo anayamba kukantha ena mwa anthuwo, amuna a Isiraeli 30,+ pamisewu ikuluikulu yakunja kwa mzinda, ndi kuwavulaza koti sakanatha kuchira. Wina mwa misewu imeneyi unali wopita ku Beteli+ ndipo wina unali wopita ku Gibeya.+ 32 Ndiyeno ana a Benjamini anayamba kunena kuti: “Tikuwagonjetsa mmene tinawagonjetsera ulendo woyamba uja.”+ Koma ana a Isiraeli anati: “Tiyeni tithawe+ kuti tiwakokere kumisewu ikuluikulu, kutali ndi mzindawu.” 33 Amuna onse a Isiraeli ananyamuka pamalo awo, n’kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ku Baala-tamara. Zili choncho, amuna a Isiraeli amene anali atabisalira+ mzinda anali kutuluka m’malo awo pafupi ndi Gibeya.+ 34 Choncho amuna osankhidwa mwapadera a Isiraeli yense, okwana 10,000 anayandikira mzinda wa Gibeya, ndipo panaulika chinkhondo choopsa. Ana a Benjamini sanadziwe kuti tsoka+ latsala pang’ono kuwagwera.

35 Yehova anagonjetsa ana a Benjamini+ pamaso pa Aisiraeli, moti pa tsiku limeneli ana a Isiraeli anapha ana a Benjamini 25,100. Onsewa anali amuna ogwira lupanga.+

36 Ana a Benjamini ataona kuti amuna a Isiraeli akuthawa,+ anaganiza kuti akugonja. Koma iwo anali kuthawa chifukwa anali kudalira amuna amene anawaika kuti abisalire mzinda wa Gibeya. 37 Ndiyeno amuna amene anabisala aja, mwamsanga anathamanga kukalowa m’Gibeya.+ Atalowa mumzindamo,+ anamwazikana ndi kukantha mzinda wonse ndi lupanga.+

38 Tsopano ana a Isiraeli anali atagwirizana ndi amuna amene anabisala aja kuti akafukize utsi mumzindamo kuti ukhale chizindikiro.+

39 Ana a Isiraeli atatembenuka ndi kuyamba kuthawa, ana a Benjamini anayamba kukantha amuna 30 mwa amuna a Isiraeli, ndi kuwavulaza moti sakanachira.+ Ana a Benjaminiwo anali kunena kuti: “Mosakayikira akugonjanso ngati mmene anagonjera pa nkhondo yoyamba ija.”+ 40 Zili choncho, utsi wa chizindikiro+ uja unayamba kukwera m’mwamba kuchokera mumzindawo, ndipo unali kuoneka ngati chipilala.+ Ana a Benjamini atatembenuka, anangoona mzinda wonse ukuyaka moto.+ 41 Pamenepo amuna a Isiraeli anatembenuka,+ ndipo ana a Benjamini anasokonezeka+ chifukwa anaona kuti tsoka lawagwera.+ 42 Tsopano ana a Benjamini anatembenuka ndi kuyamba kuthawa amuna a Isiraeli kulowera kuchipululu, moti anapanikizidwa kwambiri. Ndiyeno amuna a Isiraeli otuluka mumzinda anali kukantha ana a Benjamini pakati pawo. 43 Iwo anazungulira ana a Benjamini.+ Anawathamangitsa osawapatsa mpata wopuma.+ Anawapondaponda m’khonde mwenimweni mwa Gibeya,+ chakotulukira dzuwa. 44 Pamapeto pake, amuna 18,000 a fuko la Benjamini anaphedwa, ndipo onsewa anali amuna amphamvu zawo.+

45 Chotero anatembenuka ndi kuthawira kuchipululu, kuthanthwe la Rimoni.+ Aisiraeli anapululanso ana a Benjamini 5,000 m’misewu ikuluikulu,+ ndipo anapitiriza kuwathamangitsa mpaka kukafika ku Gidomu ndi kuphanso amuna ena 2,000. 46 Pamapeto pake, ana a Benjamini onse amene anaphedwa pa tsikulo, anakwana amuna 25,000 ogwira lupanga.+ Onsewa anali amuna amphamvu zawo. 47 Koma amuna 600 anatembenuka ndi kuthawira kuchipululu kuthanthwe la Rimoni. Iwo anapitiriza kukhala kuthanthwe la Rimoni+ kwa miyezi inayi.

48 Amuna a Isiraeli anabwerera kukaukira ana a Benjamini ndipo anakantha ndi lupanga zonse za m’mizinda, kuyambira anthu mpaka ziweto, ndi chilichonse chimene anapeza.+ Kuwonjezera apo, mizinda yonse imene anaipeza anaiyatsa moto.+

21 Tsopano amuna a Isiraeli analumbira ali ku Mizipa+ kuti: “Aliyense wa ife sadzapereka mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi mwamuna wa fuko la Benjamini.”+ 2 Ndiyeno anthuwo anapita ku Beteli+ ndi kukhala pansi kumeneko pamaso pa Mulungu woona+ mpaka madzulo. Iwo anali kulira kwambiri mofuula.+ 3 Iwo anali kunena kuti: “N’chifukwa chiyani chinthu chimenechi chachitika mu Isiraeli, inu Yehova Mulungu wa Isiraeli? N’chifukwa chiyani lero fuko limodzi lasowa mu Isiraeli?”+ 4 Ndiyeno tsiku lotsatira, anthuwo anadzuka m’mawa kwambiri ndi kumanga guwa lansembe pamenepo, ndipo anapereka nsembe zopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+

5 Kenako ana a Isiraeli anati: “Ndani mwa mafuko onse a Isiraeli amene sanabwere kwa Yehova pamodzi ndi mpingo wonse? Pajatu tinachita lumbiro lalikulu+ lokhudza aliyense amene sanabwere kwa Yehova ku Mizipa, lakuti: ‘Ameneyo aphedwe ndithu.’”+ 6 Ndipo ana a Isiraeli anayamba kumva chisoni chifukwa cha Benjamini m’bale wawo. Choncho anati: “Lero fuko limodzi ladulidwa ndi kuchotsedwa mu Isiraeli. 7 Tsopano popeza kuti ife talumbira+ pali Yehova kuti sitiwapatsa ana athu aakazi kuti akhale akazi awo,+ tichita chiyani ndi anthu amene atsala opanda akaziwa?”

8 Iwo anapitiriza kunena kuti: “Ndani mwa mafuko a Isiraeli amene sanabwere kwa Yehova ku Mizipa?”+ Pamenepo anaona kuti ku msasawo sikunabwere aliyense wochokera ku Yabesi-giliyadi+ kudzagwirizana ndi mpingowo. 9 Atawerenga anthuwo, anaona kuti panalibe ngakhale munthu mmodzi wochokera pakati pa anthu okhala ku Yabesi-giliyadi. 10 Chotero khamu la Isiraelilo linatumiza amuna amphamvu kwambiri okwana 12,000, ndipo anawalamula kuti: “Pitani, mukaphe ndi lupanga anthu okhala ku Yabesi-giliyadi. Mukaphe ngakhale akazi ndi ana aang’ono.+ 11 Zoti mukachite ndi izi: Mukaphe mwamuna aliyense komanso mkazi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna.”+ 12 Koma pakati pa anthu okhala ku Yabesi-giliyadi+ anapeza atsikana 400, anamwali+ amene anali asanagonepo ndi mwamuna. Amenewa anawabweretsa ku msasa ku Silo,+ m’dziko la Kanani.

13 Ndiyeno khamu lonse linatumiza anthu kukalankhula ndi ana a Benjamini amene anali kukhala kuthanthwe la Rimoni,+ ndi kuwalonjeza mtendere. 14 Choncho, Abenjaminiwo anabwerera pa nthawiyo. Ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga ndi moyo pakati pa akazi a ku Yabesi-giliyadi,+ koma sanawapezere akazi okwanira.+ 15 Anthuwo anamvera chisoni Abenjamini,+ chifukwa Yehova anawononga mgwirizano wa mafuko a Isiraeli. 16 Ndiyeno akulu a khamulo ananena kuti: “Tsopano popeza kuti akazi awonongedwa m’fuko la Benjamini, tichita chiyani ndi amuna amene atsala opanda akaziwa?” 17 Iwo anati: “Payenera kukhala cholowa kwa amene anathawa m’fuko la Benjamini,+ kuti fuko lililonse lisafafanizidwe mu Isiraeli. 18 Koma ife sitikuloledwa kuwapatsa ana athu aakazi kuti akhale akazi awo, chifukwa ana a Isiraeli analumbira kuti, ‘Aliyense wopereka mkazi kwa mwamuna wa fuko la Benjamini ndi wotembereredwa.’”+

19 Pamapeto pake anati: “Pajatu ku Silo+ kumachitika chikondwerero cha Yehova chaka ndi chaka. Mzinda wa Silo uli kum’mwera kwa Beteli, chakum’mawa kwa msewu waukulu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu,+ ndiponso chakum’mwera kwa Lebona.” 20 Choncho analamula ana a Benjamini kuti: “Pitani, mukawabisalire m’minda ya mpesa. 21 Ndiyeno mukakaona ana aakazi a ku Silo akubwera kuti adzavine+ magule ovina mozungulira, mukavumbuluke m’minda ya mpesayo, ndipo aliyense akagwire mkazi mokakamiza pakati pa ana aakazi a ku Silo, ndi kupita nawo kudziko la Benjamini. 22 Abambo awo kapena abale awo akabwera kudzatiimba mlandu, tidzawauza kuti, ‘Tikomereni mtima powathandiza iwowa, chifukwa chakuti panthawi ya nkhondo, ife sitinagwire akazi okwanira Abenjamini onse.+ Ndipotu inu simunawapatse ana anuwo kapena alongo anuwo mwa kufuna kwanu, zimene zikanachititsa kuti mukhale ndi mlandu chifukwa cha lumbiro limene tinapanga lija.’”+

23 Chotero ana a Benjamini anachitadi zomwezo. Pakati pa akazi amene anali kuvina+ mozungulira, anagwirapo akazi okwanira chiwerengero chawo.+ Atatero, anachoka ndi kubwerera kumalo awo ndipo anamanga mizinda+ ndi kukhalamo.

24 Pa nthawiyo, ana a Isiraeli anayamba kumwazikana kuchoka kumeneko, aliyense anapita ku fuko lake ndi ku banja lake. Iwo anachoka kumeneko, moti aliyense anapita ku cholowa chake.+

25 Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Aliyense anali kuchita zimene anali kuona kuti n’zoyenera.+

Kapena kuti, “Kenako anatsetsereka (anatsika) pabulupo.”

Dzinali limatanthauza, “Dera la Madzi.”

Onani mawu a m’munsi pa Nu 21:3.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Dzinali limatanthauza, “Olira.”

Kapena kuti, “Timinati-sera.”

“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Koma ena amakhulupirira kuti lupanga limeneli kutalika kwake linali masentimita 38.

Kapena kuti, “mafano osema.”

Kapena kuti, “patsindwi.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

“Hatchi” ena amati “hosi” kapena “kavalo.”

Pawindo limeneli panali potchingidwa ndi timatabwa tolukanalukana.

Mawu akuti “banja lathu” mawu ake enieni ndi “sauzande yanga.”

“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.

Dzinali limatanthauza kuti, “Yehova ndi Mtendere.”

Dzinali limatanthauza kuti, “Baala Adziweruzire Yekha Mlandu wa Munthuyu.”

“Ulonda wapakati pa usiku” unali kuyamba 10 koloko usiku mpaka 2 koloko usiku.

Ena amati “masikiyo.”

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Mawu ake enieni, “anayamba kuchita nacho chiwerewere.”

Ameneyu ndi Gidiyoni. Onani Owe 6:32.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Dzinali limatanthauza, “Mwini Pangano,” kapena “Baala wa Pangano.”

Dzinali limatanthauza, “Ochita Zamatsenga.” Onani De 18:14.

Dzinali limatanthauza, “Mulungu wa pangano.” Ameneyu ndi Baala wa ku Sekemu.

Ena amati “kugwaza.”

Dzinali limatanthauza, “Midzi ya Mahema ya Yairi.”

Mawu ake enieni, “ndinaika moyo wanga m’dzanja langa.”

Mawu ake enieni, “kuwakantha, n’kuunjika miyendo ndi ntchafu pamodzi.”

Dzinali limatanthauza, “Malo Okwezeka a Fupa la Nsagwada.”

Dzinali limatanthauza, “Kasupe wa Munthu Wofuula.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

Onani mawu a m’munsi pa Gen 31:19.

Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.

Dzinali limatanthauza, “Msasa wa Dani.”

Mawu ake enieni, “anali kutha kuponya mwala n’kulasa tsitsi limodzi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena