Nyimbo ya Solomo
1 Nyimbo yokoma kwambiri,+ nyimbo ya Solomo:+ 2 “Undipsompsone ndi milomo yako,+ chifukwa chikondi chimene umandisonyeza chimaposa vinyo kukoma kwake.+ 3 Mafuta+ ako odzola ndi onunkhira bwino. Dzina lako lili ngati mafuta othira pamutu.+ N’chifukwa chake atsikana amakukonda. 4 Nditenge,+ tiye tithawe! Chifukwatu mfumu yandipititsa m’zipinda zake zamkati.+ Tiye tikondwere ndi kusangalalira limodzi. Tiye tinene za chikondi chimene umandisonyeza osati za vinyo.+ M’pake kuti atsikana amakukonda.+
5 “Inu ana aakazi a ku Yerusalemu,+ ine ndine mtsikana wakuda ngati mahema a ku Kedara,+ koma wokongola ngati nsalu za mahema+ a Solomo. 6 Musandiyang’anitsitse chifukwa chakuti ndada, ndi dzuwatu landidetsali. Pakuti ana aamuna a mayi anga anandikwiyira. Choncho anandiika kuti ndiziyang’anira minda ya mpesa moti sindinathe kuyang’anira munda wangawanga wa mpesa.+
7 “Iwe amene mtima wanga umakukonda,+ tandiuza kumene umakadyetsera ziweto,+ kumene umakagonetsa ziweto masana. Kodi ndikhalirenji ngati mkazi amene wafunda nsalu ya namalira pakati pa magulu a ziweto za anzako?”
8 “Ngati iweyo sukudziwa, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse,+ tsatira mapazi a ziweto ndipo ukadyetse ana ako a mbuzi pafupi ndi mahema a abusa.”
9 “Kwa ine, wokondedwa wangawe+ ndiwe wokongola ngati hatchi* yaikazi ya pamagaleta* a Farao.+ 10 Masaya ako ndi okongola pakati pa tsitsi lako lomanga, ndipo khosi lako lovala mkandalo limaoneka bwino.+ 11 Ife tikupangira zokongoletsa zoti uzivala kumutu. Zokongoletsazo zikhala zozungulira, zagolide,+ zokhala ndi mikanda yasiliva.”
12 “Pamene mfumu yakhala patebulo lake lozungulira, fungo labwino la nado*+ wanga likumveka kwa wokondedwa wanga.+ 13 Wachikondi wanga ali ngati kathumba ka mule*+ kwa ine. Iye adzakhala pakati pa mabere anga+ usiku wonse. 14 Kwa ine, wachikondi wanga ali ngati duwa lofiirira+ m’minda ya mpesa ya ku Eni-gedi.”+
15 “Ndiwe wokongola kwabasi, wokondedwa wanga.+ Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa.”+
16 “Iwenso ndiwe wokongola,+ wachikondi wanga. Ndiwe mnyamata wosangalatsa kwambiri. Bedi+ lathunso ndi la masamba ofewa. 17 Nyumba yathu yokongola inamangidwa ndi mitengo ya mkungudza,+ ndipo kudenga* kwake kuli mitengo yofanana ndi mkungudza.
2 “Ine ndine duwa lonyozeka+ la m’chigwa cha m’mphepete mwa nyanja.+ Inetu ndine duwa la m’chigwa.”+
2 “Monga duwa pakati pa zitsamba zaminga, ndi mmene alili wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.”+
3 “Monga mtengo wa maapozi+ pakati pa mitengo ya m’nkhalango, ndi mmene alili wachikondi wanga pakati pa ana aamuna.+ Ineyo ndinali kulakalaka mthunzi wa wokondedwa wanga ndipo ndinakhala pansi, pamthunzi wakewo. Chipatso chake chinali chotsekemera* m’kamwa mwanga. 4 Iye anandipititsa kunyumba ya phwando la vinyo,+ ndipo chikondi+ chake kwa ine chinali ngati mbendera+ yozikidwa pambali panga. 5 Anthu inu ndipatseni mphesa zouma zoumba pamodzi kuti zinditsitsimule.+ Ndipatseni maapozi kuti ndisafe chifukwa chikondi chikundidwalitsa.+ 6 Dzanja lake lamanzere lili pansi pa mutu wanga, ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.+ 7 Ndakulumbiritsani inu+ ana aakazi a ku Yerusalemu, pali mbawala zazikazi+ ndiponso pali mphoyo+ zakutchire, kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.+
8 “Ndikumva wachikondi wanga+ akubwera.+ Akukwera mapiri ndipo akudumphadumpha pazitunda. 9 Wachikondi wanga akufanana ndi mbawala+ kapena mphoyo yaing’ono. Taonani! Iye waima kuseri kwa khoma* la nyumba yathu. Akuyang’ana m’mawindo,* akusuzumira pa zotchingira m’mawindo.+ 10 Wachikondi wanga wandiuza kuti, ‘Nyamuka wokondedwa wanga wokongolawe,+ tiye tizipita.+ 11 Taona! Nyengo yamvula yatha,+ mvula yaleka, yapita kwawo. 12 Maluwa ayamba kuoneka m’dziko,+ nthawi yodulira mpesa+ yakwana, ndipo m’dziko lathu mukumveka kulira kwa njiwa.+ 13 Pamtengo wa mkuyu,+ nkhuyu zoyambirira zapsa.+ Mpesa wachita maluwa ndipo ukununkhira. Nyamuka, bwera kuno wokondedwa wanga+ wokongola, tiye tizipita. 14 Iwe njiwa yanga,+ tuluka m’malo obisika a pathanthwe. Tuluka pamalo osaoneka m’mphepete mwa njira yotsetsereka. Ndikufuna ndione thupi lako lokongola.+ Ndikufuna kumva mawu ako, chifukwa mawu ako ndi okoma ndipo iweyo ndiwe wokongola.’”+
15 “Anthu inu mutigwirire nkhandwe+ zing’onozing’ono zimene zikuwononga minda ya mpesa, chifukwa minda yathu ya mpesa yachita maluwa.”+
16 “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.+ Iye akudyetsera ziweto msipu+ umene uli pakati pa maluwa am’tchire.+ 17 Mpaka nthawi ya kamphepo kayaziyazi ndiponso mpaka mithunzi itachoka, tembenuka wachikondi wanga. Ukhale ngati mbawala+ kapena ngati mphoyo yaing’ono pamapiri amene akutilekanitsa.
3 “Pabedi panga usiku, ndinaganizira za munthu amene mtima wanga umam’konda.+ Ndinalakalaka kumuona koma iye panalibe. 2 Chotero ndinati: ‘Ndidzuke ndikazungulire mumzinda,+ m’misewu ndi m’mabwalo a mumzinda,+ kuti ndikafunefune munthu amene mtima wanga umam’konda.’ Ndinam’funafuna koma sindinamupeze. 3 Alonda+ amene anali kuzungulira mumzindawo anandipeza, ndipo ine ndinawafunsa kuti: ‘Kodi amuna inu, mwamuonako munthu amene mtima wanga umam’konda?’ 4 Nditangowapitirira pang’ono, ndinam’peza munthu amene mtima wanga umam’konda. Ndinamugwira ndipo sindinafune kum’siya mpaka nditamubweretsa m’nyumba mwa mayi anga, m’chipinda chamkati cha mayi amene anali ndi pakati kuti ine ndibadwe. 5 Ndakulumbiritsani inu+ ana aakazi a ku Yerusalemu, pali mbawala zazikazi ndiponso pali mphoyo zakutchire,+ kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.”+
6 “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi n’chiyani, chooneka ngati utsi wokwera m’mwamba, chonunkhira mafuta a mule, lubani,*+ ndi mtundu uliwonse wa zonunkhira za ufa za munthu wamalonda?”+
7 “Taonani! Ndi bedi la Solomo. Amuna 60 amphamvu ochokera mwa amuna amphamvu a Isiraeli alizungulira.+ 8 Onsewo atenga malupanga ndipo ndi ophunzitsidwa nkhondo. Aliyense wamangirira lupanga lake m’chiuno mwake kuti adziteteze ku zoopsa za usiku.”+
9 “Ndi bedi* limene Mfumu Solomo inadzipangira ndi mitengo ya ku Lebanoni.+ 10 Mizati yake ndi yasiliva. Motsamira mwake ndi mwagolide. Pokhalira pake ndi popangidwa ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. Mkati mwake, ana aakazi a ku Yerusalemu akongoletsamo posonyeza chikondi.”
11 “Inu ana aakazi a Ziyoni, pitani panja mukaone Mfumu Solomo itavala nkhata yamaluwa,+ imene mayi ake+ anailukira pa tsiku la ukwati wake, pa tsiku limene mtima wa mfumuyo unasangalala.”+
4 “Ndiwe wokongola kwabasi,+ wokondedwa wanga. Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa+ munsalu yako yophimba kumutuyo.+ Tsitsi lako likuoneka ngati gulu la mbuzi+ zimene zikudumphadumpha potsetsereka kuchokera kudera lamapiri la Giliyadi.+ 2 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zazikazi zomwe angozimeta kumene,+ zimene zikuchokera kozisambitsa, zonse zitabereka mapasa, popanda imene ana ake afa. 3 Milomo yako ili ngati chingwe chofiira kwambiri, ndipo kulankhula kwako n’kosangalatsa.+ M’mbali mwa mutu wako muli ngati khangaza* logamphula pakati, munsalu yako yophimba kumutuyo.+ 4 Khosi lako+ lili ngati nsanja+ ya Davide. Lili ngati nsanja yomangidwa ndi miyala yokhala m’mizeremizere, yomwe akolekapo zishango 1,000, zishango zonse zozungulira+ za amuna amphamvu. 5 Mabere ako awiri+ ali ngati ana awiri aang’ono, ngati ana amapasa a insa yaikazi, amene akudya msipu pakati pa maluwa akutchire.”+
6 “Nthawi ya kamphepo kayaziyazi isanakwane+ ndiponso mithunzi isanachoke, ndipita kuphiri la mule ndiponso kuphiri la lubani.”+
7 “Ndiwe wokongola paliponse,+ wokondedwa wanga, ndipo mwa iwe mulibe chilema chilichonse.+ 8 Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni, iwe mkwatibwi wanga,+ tiye tichoke ku Lebanoni.+ Utsetsereke kuchokera pamwamba pa phiri la Amana, kuchokera pamwamba pa phiri la Seniri,+ ngakhalenso pamwamba pa phiri la Herimoni.+ Utsetsereke kuchokera m’mapanga a mikango, ndiponso kuchokera kumapiri a akambuku.* 9 Wachititsa mtima wanga kugunda, iwe mlongo wanga,+ mkwatibwi wanga.+ Wachititsa mtima wanga kugunda ndi diso lako limodzi lokha,+ ndiponso ndi diso limodzi lokha la mkanda wa m’khosi mwako. 10 Chikondi chimene umandisonyeza n’chokoma,+ iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga. Chikondi chimene umandisonyeza n’chabwino kuposa vinyo ndipo kununkhira kwa mafuta ako odzola n’koposa zonunkhira za mitundu yonse.+ 11 Milomo yako imangokhalira kukha uchi wapachisa,+ iwe mkwatibwi wanga. Uchi+ ndi mkaka zili kuseri kwa lilime lako, ndipo kununkhira kwa zovala zako kuli ngati kununkhira+ kwa nkhalango ya Lebanoni. 12 Mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ali ngati munda wotchingidwa ndi mpanda.+ Iye ali ngati munda wotchingidwa ndi mpanda, ndiponso ngati kasupe wotsekedwa. 13 Khungu lako lili ngati munda wokongola* wokhala ndi mitengo ya makangaza ya zipatso zabwino kwambiri,+ mitengo ya maluwa ofiirira, mitengo ya nado,+ 14 maluwa a safironi,+ mabango onunkhira,+ sinamoni,+ komanso mitengo yosiyanasiyana ya lubani, mule, aloye,+ ndi zonunkhira zonse zabwino kwambiri.+ 15 Khungu lako lilinso ngati kasupe wa m’munda, chitsime cha madzi abwino,+ ndiponso timitsinje tochokera ku Lebanoni.+ 16 Dzuka, iwe mphepo yakumpoto. Bwera, iwe mphepo yakum’mwera.+ Womba pamunda wanga+ kuti kununkhira kwake kumveke.”
“Wachikondi wanga alowe m’munda wake kuti adzadye zipatso zake zokoma kwambiri.”
5 “Ndabwera m’munda mwanga,+ iwe mlongo wanga,+ mkwatibwi wanga.+ Ndathyola mule+ wanga limodzi ndi zonunkhiritsa zanga. Ndadya chisa changa cha uchi limodzi ndi uchi wanga.+ Ndamwa vinyo wanga limodzi ndi mkaka wanga.”
“Idyani, inu anthu okondana! Imwani ndipo muledzere ndi chikondi chimene mukusonyezana.”+
2 “Panopa ndili m’tulo koma mtima wanga uli maso.+ Ndikumva wachikondi wanga akugogoda.”+
“Nditsegulire+ iwe mlongo wanga, wokondedwa wanga, njiwa yanga, iwe wopanda chilema.+ Pakuti m’mutu mwanga mwadzaza mame, ndipo tsitsi langa ladzaza madontho a madzi a usiku.”+
3 “‘Ndavula mkanjo wanga. Kodi ndiuvalenso? Ndatsuka mapazi anga. Kodi ndiwadetsenso?’ 4 Wachikondi wanga atachotsa dzanja lake pabowo la chitseko, m’mimba mwanga+ munabwadamuka. 5 Ine ndinadzuka kuti ndimutsegulire wachikondi wanga ndipo manja anga anali kuyenderera mafuta a mule. Zala zanga zinali kuyenderera mule pamene ndinali kugwira pabowo lolowetsapo loko wa pachitseko. 6 Ndinam’tsegulira wachikondi wanga, koma wachikondi wangayo anali atachokapo, atapita. Moyo wanga unachoka mwa ine nditamva mawu ake. Ndinam’funafuna koma sindinam’peze.+ Ndinamuitana koma sanandiyankhe. 7 Alonda+ amene anali kuyendayenda mumzinda anandipeza. Anandimenya, anandivulaza. Alonda a pamipanda+ anandilanda chofunda changa.
8 “Ndakulumbiritsani+ inu ana aakazi a ku Yerusalemu+ kuti mukam’peza wachikondi wanga,+ mumuuze kuti ine chikondi chikundidwalitsa.”+
9 “Kodi wachikondi wako akuposa bwanji achikondi ena onse,+ iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse?+ Kodi wachikondi wako akuposa bwanji achikondi ena onse, kuti utilumbiritse lumbiro lotereli?”+
10 “Wachikondi wanga ndi wokongola ndipo khungu lake ndi lofiirira. Pa amuna 10,000, iye ndiye wooneka bwino kwambiri.+ 11 Mutu wake ndi wokongola ngati golide, golide woyengedwa bwino. Tsitsi lake lili ngati zipatso za kanjedza. Tsitsi lakelo ndi lakuda ngati khwangwala. 12 Maso ake ali ngati njiwa zimene zili pafupi ndi mtsinje wamadzi, zimene zikusamba mumkaka, zitakhala chakumphepete kwa madziwo. 13 Masaya ake ali ngati bedi la m’munda la maluwa onunkhira,+ ndiponso ngati nsanja zomangidwa ndi zitsamba zonunkhira. Milomo yake ili ngati maluwa amene akuchucha mafuta a mule.+ 14 Zala zake zonenepa bwino ndi zagolide, ndipo zikhadabo zake ndi zakulusolito. Mimba yake ndi yopangidwa ndi minyanga ya njovu yokutidwa ndi miyala ya safiro. 15 Miyendo yake ili ngati zipilala zamiyala ya mabo zozikidwa pazitsulo zokhala ndi mphako, zagolide woyengedwa bwino. Iye ndi wokongola ngati dziko la Lebanoni ndipo palibe wofanana naye pa nkhani ya kukongola, mofanana ndi mitengo ya mkungudza.+ 16 M’kamwa mwake ndi mokoma kwambiri ndipo chilichonse mwa iye n’chosiririka.+ Ameneyu ndiye wachikondi wanga ndipo ameneyutu ndiye wokondedwa wanga, inu ana aakazi a ku Yerusalemu.”
6 “Kodi wachikondi wako wapita kuti, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse?+ Kodi wachikondi wako walowera kuti, kuti tikuthandize kum’funafuna?”
2 “Wachikondi wanga watsetserekera kumunda wake,+ kumabedi am’munda a maluwa onunkhira,+ kuti akadyetse ziweto+ kuminda, ndiponso kuti akathyole maluwa. 3 Wachikondi wangayo, ine ndine wakewake ndipo iye ndi wangawanga.+ Iye akudyetsera ziweto msipu+ umene uli pakati pa maluwa.”
4 “Wokondedwa wangawe, ndiwe wokongola+ ngati Mzinda Wosangalatsa.+ Ndiwe wooneka bwino ngati Yerusalemu,+ ndipo ndiwe wogometsa ngati magulu a asilikali+ amene azungulira mbendera.+ 5 Yang’ana kumbali kuti maso ako+ asandiyang’anitsitse, chifukwa akundichititsa mantha. Tsitsi lako likuoneka ngati gulu la mbuzi zimene zikudumphadumpha potsetsereka kuchokera ku Giliyadi.+ 6 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zazikazi zimene zikuchokera kozisambitsa, zonse zitabereka mapasa, popanda imene ana ake afa.+ 7 M’mbali mwa mutu wako muli ngati khangaza logamphula pakati, munsalu yako yophimba kumutuyo.+ 8 Pakati pa mafumukazi 60, adzakazi* 80 ndi atsikana osawerengeka,+ 9 pali mmodzi yekha amene ali njiwa yanga,+ wopanda chilema.+ Iye ndiye mwana wamkazi wapadera kwambiri kwa mayi ake. Iyeyo ndi wosadetsedwa kwa mayi amene anam’bereka. Ana aakazi atamuona, anamutcha wodala. Mafumukazi ndi adzakazi anamutamanda+ kuti, 10 ‘Kodi mkazi+ amene akuyang’ana pansi ngati m’bandakuchayu ndani,+ wokongola ngati mwezi wathunthu,+ wosadetsedwa ngati dzuwa lowala,+ wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera?’”+
11 “Ine ndinatsetserekera kumunda+ wa mitengo ya zipatso zokhala ngati mtedza, kuti ndikaone maluwa ake m’chigwa,*+ kuti ndikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira, ndiponso ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.+ 12 Mosazindikira, mtima wanga unandifikitsa kumagaleta a anthu olemekezeka a mtundu wanga.”
13 “Bwerera, bwerera iwe Msulami! Bwerera, bwerera kuti tikuone!”+
“Kodi anthu inu mukuona chiyani mwa ine Msulami?”+
“Tikuona ngati tikuonerera gule wa magulu awiri a anthu.”
7 “Mapazi ako akukongola kwambiri munsapato zako,+ iwe mwana wamkazi+ wodzipereka. Ntchafu zako n’zoumbidwa bwino ngati zinthu zokongoletsera,+ ngati ntchito ya manja a munthu waluso. 2 Mchombo wako uli ngati mbale yozungulira. Vinyo wosakaniza+ asasowepo. Mimba yako ili ngati mulu wa tirigu, wotchingidwa ndi maluwa.+ 3 Mabere ako awiri ali ngati ana awiri aang’ono, ngati ana amapasa a insa yaikazi.+ 4 Khosi lako+ lili ngati nsanja ya mnyanga wa njovu. Maso ako+ ali ngati maiwe a ku Hesiboni,+ amene ali pafupi ndi chipata cha Bati-rabimu. Mphuno yako ili ngati nsanja ya Lebanoni, imene inayang’ana cha ku Damasiko. 5 Mutu wako ndi wokwezeka ngati Karimeli.+ Tsitsi+ la m’mutu mwako lili ngati ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira,+ ndipo mfumu yatengeka nalo tsitsi lako lalitalilo.+ 6 Iwe mtsikana wokondedwa, ndiwe wokongola, ndipo ndiwe wosangalatsa kuposa zinthu zina zonse zosangalatsa mtima.+ 7 Msinkhu wako uli ngati mtengo wa kanjedza,*+ ndipo mabere ako+ ali ngati zipatso zake. 8 Ine ndinati, ‘Ndikwera mtengo wa kanjedza kuti ndikathyole nthambi zake zokhala ndi zipatso.’+ Mabere ako akhale ngati zipatso za mpesa, ndipo mpweya wa m’kamwa mwako ununkhire ngati maapozi. 9 M’kamwa mwako mukhale ngati vinyo wabwino kwambiri+ amene amatsetserekera kukhosi kwa wokondedwa wanga mwamyaa,+ amene amayenderera pang’onopang’ono pamilomo ya anthu amene akugona.”
10 “Wachikondi wangayo, ine ndine wake,+ ndipo iye akulakalaka ineyo.+ 11 Bwera wachikondi wanga. Tiye tipite kumunda.+ Tiye tikakhale pakati pa mitengo ya maluwa ofiirira.+ 12 Tiye tilawirire m’mawa tipite kuminda ya mpesa. Tikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,+ ngati yatuluka maluwa,+ ndiponso ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.+ Kumeneko ndikakusonyeza chikondi changa.+ 13 Zipatso za mandereki*+ zikununkhira, ndipo pafupi ndi makomo olowera kunyumba zathu pali zipatso zosiyanasiyana zokoma kwambiri.+ Ndakusungira zipatso zatsopano ndi zakale zomwe, iwe wachikondi wanga.
8 “Ndikulakalaka ukanakhala ngati mlongo wanga,+ amene anayamwa mabere a mayi anga.+ Ndikanakupeza panja ndikanakupsompsona,+ ndipo anthu sakanandinyoza n’komwe. 2 Bwenzi nditakutsogolera ndipo ndikanakulowetsa m’nyumba mwa mayi anga,+ amene ankandiphunzitsa. Ndikanakupatsa vinyo wothira zonunkhiritsa,+ ndi madzi a makangaza ongofinya kumene. 3 Dzanja lake lamanzere likanakhala pansi pa mutu wanga, ndipo dzanja lake lamanja likanandikumbatira.+
4 “Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu, kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.”+
5 “Kodi mkazi+ amene akuchokera kuchipululuyu ndani,+ atakoloweka dzanja lake m’khosi mwa wachikondi wake?”+
“Ine ndinakudzutsa pansi pa mtengo wa maapozi. Pamenepo m’pamene mayi ako anamva zowawa pokubereka. Mayi amene anali kukubereka anamva zowawa ali pamenepo.+
6 “Undiike pamtima pako ngati chidindo,+ ndiponso undiike ngati chidindo padzanja lako, chifukwa chikondi n’champhamvu ngati imfa.+ Mofanana ndi Manda,* chikondi sichigonja ndipo chimafuna kudzipereka ndi mtima wonse.+ Kuyaka kwake kuli ngati kuyaka kwa moto. Chikondicho ndi lawi la Ya.*+ 7 Madzi ambiri sangathe kuzimitsa chikondi,+ ndipo mitsinje singachikokolole.+ Munthu atapereka zinthu zonse zamtengo wapatali za m’nyumba mwake posinthanitsa ndi chikondi, anthu anganyoze zinthuzo.”
8 “Tili ndi mlongo wathu wamng’ono+ amene alibe mabere. Kodi tidzamuchitire chiyani tsiku limene adzafunsiridwe ukwati?”
9 “Akadzakhala khoma,+ tidzam’mangira kansanja kasiliva pamwamba pake, koma akadzakhala chitseko,+ tidzam’khomerera ndi thabwa la mkungudza.”
10 “Ine ndine khoma, ndipo mabere anga ali ngati nsanja.+ Choncho m’maso mwake ndakhala ngati mkazi amene wapeza mtendere.
11 “Solomo anali ndi munda wa mpesa+ ku Baala-hamoni. Munda wa mpesawo anaupereka kwa anthu oti aziusamalira.+ Munthu aliyense anali kubweretsa ndalama zasiliva zokwana 1,000 zolipirira zipatso za mundawo.
12 “Munda wanga wa mpesa ndingathe kuchita nawo chilichonse. Ndalama 1,000 zasilivazo ndi zanu inu a Solomo, ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za anthu amene amatenga zipatso za munda wanu wa mpesa.”
13 “Iwe amene ukukhala m’minda,+ anzanga* akufuna amve mawu ako. Inenso ndikufuna ndimve mawu ako.”+
14 “Thamanga wachikondi wanga. Ukhale ngati insa kapena ngati mphoyo yaing’ono pamapiri pamene pamamera maluwa onunkhira.”+
Ena amati “hosi,” kapena “kavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Chimenechi ndi chitsamba chinachake chonunkhira bwino.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “tsindwi.”
Ena amati “chonzuna.”
Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
Pawindo limeneli panali potchingidwa ndi timatabwa tolukanalukana.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Limeneli linali bedi lochita kunyamula, limene anali kunyamulirapo munthu wolemekezeka.
“Khangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
Ena amati “anyalugwe.”
Mawu ake enieni, “paradaiso.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Umenewu ndi mtundu wa kanjedza amene amamera ku Palesitina.
“Mandereki” ndi chitsamba cha m’gulu la mbatata, chimene chimabereka zipatso.
Onani Zakumapeto 5.
Awa ndi malo okhawo m’buku la Nyimbo ya Solomo pamene pakupezeka dzina la Mulungu. Panopa, lalembedwa mwachidule kuti “Ya.” Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2 ndi Zakumapeto 1.
Mwina akutanthauzanso, “anzako.”