Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Ecclesiastes 1:1-12:14
  • Mlaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mlaliki
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Mlaliki

Mlaliki*

1 Mawu a wosonkhanitsa anthu,+ mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu.+ 2 Wosonkhanitsa anthu wanena kuti: “Zachabechabe!+ Zinthu zonse n’zachabechabe!”+ 3 Kodi munthu amapeza phindu lanji pa ntchito yake yonse yovuta, imene amaigwira+ mwakhama padziko lapansi pano?*+ 4 M’badwo umapita+ ndipo m’badwo wina umabwera,+ koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.*+ 5 Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa,+ kenako limathamanga mwawefuwefu kupita kumalo ake kuti likatulukenso.+

6 Mphepo imapita kum’mwera ndipo imazungulira n’kupita kumpoto.+ Iyo imangozungulirazungulira+ mpaka imabwereranso kumene inayambira kuzungulira.+

7 Mitsinje*+ yonse imapita kunyanja+ koma nyanjayo sidzaza.+ Mitsinjeyo imabwerera kumalo kumene inachokera kuti ikayambirenso kuyenda.+ 8 Zinthu zonse n’zotopetsa,+ ndipo palibe angazifotokoze. Diso silikhuta n’kuona,+ ndipo khutu silidzaza chifukwa cha kumva.+ 9 Zimene zinalipo n’zimene zidzakhaleponso+ ndipo zimene zinachitidwa n’zimene zidzachitidwenso. Choncho palibe chatsopano padziko lapansi pano.+ 10 Kodi chilipo chimene munthu anganene kuti: “Wachiona ichi, n’chatsopanotu chimenechi?” Ayi, chakhalapo kuyambira kalekale.+ Zimene zilipo panopa, zinalipo ife tisanakhaleko.+ 11 Anthu akale sakumbukiridwa, ndipo amene adzakhalepo m’tsogolo sadzakumbukiridwanso.+ Iwowanso sadzakumbukiridwa ndi amene adzakhalepo m’tsogolo mwawo.+

12 Ine wosonkhanitsa, ndinali mfumu ya Isiraeli ku Yerusalemu.+ 13 Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndifunefune ndi kufufuza nzeru+ mogwirizana ndi zonse zimene zachitidwa padziko lapansi, kutanthauza ntchito yosautsa mtima imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira.+ 14 Choncho ndinaona ntchito zonse zimene zinachitidwa padziko lapansi pano,+ ndipo ndinapeza kuti zonse ndi zachabechabe ndiponso zili ngati kuthamangitsa mphepo.+

15 Chinthu chokhota sichingawongoledwe+ ndipo chimene palibe sichingawerengedwe n’komwe. 16 Ineyo ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Ine ndili ndi nzeru zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+ Komanso mtima wanga wapeza nzeru zambiri ndiponso wadziwa zinthu zambiri.”+ 17 Ndinapereka mtima wanga kuti udziwe nzeru ndiponso misala,+ ndipo ndadziwa uchitsiru.+ Pochita zimenezi ndazindikira kuti zimenezinso zili ngati kuthamangitsa mphepo.+ 18 Pakuti nzeru zikachuluka pamachulukanso kukhumudwa,+ choncho amene amadziwa zinthu zambiri amakhalanso ndi zopweteka zambiri.+

2 Ine ndinadziuza mumtima mwanga+ kuti: “Ndiyesereko kusangalala.+ Komanso ndisangalale ndi zinthu zabwino.”+ Ndipo ndinaona kuti zimenezonso zinali zachabechabe. 2 Ndinauza kuseka kuti: “Ndiwe wamisala!”+ ndipo kusangalala+ ndinakuuza kuti: “Uli ndi phindu lanji?”

3 Ndinafufuza ndi mtima wanga wonse kuti ndidziwe uchitsiru posangalatsa thupi langa ndi vinyo,+ pamene ndinali kutsogolera mtima wanga ndi nzeru.+ Ndinachita zimenezi kuti ndione ubwino umene ana a anthu amapeza pa zimene amachita padziko lapansi pano masiku onse a moyo wawo.+ 4 Ndinachita zinthu zikuluzikulu.+ Ndinadzimangira nyumba zambirimbiri.+ Ndinalima minda ya mpesa yambirimbiri.+ 5 Ndinadzipangira minda yokongola ndi malo obzalamo maluwa ndi mitengo.+ Mmenemu ndinabzalamo mitengo ya zipatso zosiyanasiyana. 6 Ndinadzipangira madamu a madzi+ kuti ndizithirira mitengo imene inali kumera m’nkhalango yanga.+ 7 Ndinali ndi antchito aamuna ndi aakazi.+ Ndinalinso ndi antchito obadwira m’nyumba mwanga.+ Komanso, ndinali ndi ziweto zochuluka zedi, ng’ombe ndi nkhosa. Ziwetozo zinali zambiri kuposa za onse amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+ 8 Ndinapezanso siliva ndi golide wambiri,+ ndi chuma chimene chimakhala ndi mafumu ndiponso chimene chimapezeka m’zigawo za dziko.+ Ndinali ndi oimba aamuna ndi aakazi.+ Ndinalinso ndi akazi ambiri,+ omwe amasangalatsa mtima+ wa amuna. 9 Ndinali ndi zinthu zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+ Komanso ndinali kuchitabe zinthu mwanzeru.+

10 Chilichonse chimene maso anga anali kupempha sindinali kuwamana.+ Mtima wanga sindinaumane chosangalatsa cha mtundu uliwonse. Ndinasangalalanso ndi ntchito yonse imene ndinaigwira mwakhama.+ Imeneyi ndiyo inali mphoto yanga ya ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama.+ 11 Ineyo ndinaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse.+ Nditatero, ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe ndipo kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+

12 Ineyo ndinaganizaganiza kuti nzeru n’chiyani,+ misala n’chiyani, ndipo uchitsiru n’chiyani.+ Kodi munthu wochokera kufumbi amene wabwera pambuyo pa mfumu angachite chiyani? Zimene angachite n’zimene anthu ena anachita kale. 13 Ndinaona kuti nzeru zili ndi phindu lalikulu kuposa uchitsiru+ monga mmene kuwala kulili ndi phindu lalikulu kuposa mdima.+

14 Aliyense wanzeru maso ake amaona bwino,+ koma wopusa amangoyendabe mu mdima waukulu.+ Ineyo ndazindikira kuti onsewa mapeto awo ndi amodzi.+ 15 Ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Mapeto ngati a munthu wopusa+ adzagweranso ineyo ndithu.”+ Choncho kodi ineyo ndinavutikiranji kukhala wanzeru kwambiri+ pa nthawi imene ija? Ndipo ndinanena mumtima mwanga kuti: “Izinso n’zachabechabe.” 16 Pakuti munthu wanzeru, mofanana ndi wopusa, sadzakumbukiridwa mpaka kalekale.+ M’masiku amene akubwerawa aliyense adzaiwalidwa. Ndipo kodi wanzeru adzafa motani? Adzafa mofanana ndi wopusa.+

17 Ine ndinadana ndi moyo+ chifukwa ndinaona kuti ntchito imene yachitidwa padziko lapansi pano ndi yosautsa mtima.+ Pakuti zonse zinali zachabechabe ndipo kuchita zimenezi kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ 18 Ineyo ndinadana ndi ntchito yonse yovuta imene ndinali kugwira padziko lapansi pano,+ imene ndidzasiyire munthu amene akubwera pambuyo panga.+ 19 Ndipo kodi ndani angadziwe kuti kaya adzakhala wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinazipeza movutikira ndiponso zimene ndinazichita mwanzeru padziko lapansi pano.+ Zimenezinso n’zachabechabe. 20 Ineyo ndinayamba kutaya mtima+ poganizira ntchito yanga yonse yovuta imene ndinaigwira mwakhama padziko lapansi pano. 21 Pakuti pali munthu amene ntchito yake yovuta waigwira mwanzeru, mozindikira ndiponso waigwira bwino.+ Koma zonse zimene anapeza zidzaperekedwa kwa munthu amene sanagwire mwakhama ntchito ngati imeneyo.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo n’zomvetsa chisoni kwambiri.+

22 Pakuti munthu amapeza chiyani pa ntchito yonse imene waigwira mwakhama, ndiponso imene wasautsika nayo mtima poigwira padziko lapansi pano?+ 23 Masiku ake onse, ntchito yakeyo imamubweretsera zowawa ndi zokhumudwitsa.+ Komanso usiku mtima wake sugona.+ Izinso n’zachabechabe.

24 Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Ineyo ndaona kuti zimenezinso n’zochokera m’dzanja la Mulungu woona.+ 25 Pakuti ndani amadya+ bwino ndi kumwa zabwino kuposa ine?+

26 Munthu wabwino pamaso pa Mulungu,+ Mulunguyo amam’patsa nzeru, kudziwa zinthu, ndi kusangalala.+ Koma wochimwa amam’patsa ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa zinthu kuti azipereke kwa munthu amene ali wabwino pamaso pa Mulungu woona.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo kuli ngati kuthamangitsa mphepo.+

3 Chilichonse chili ndi nthawi yake,+ ndipo chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake: 2 Pali nthawi yobadwa+ ndi nthawi ya kufa.+ Nthawi yobzala ndi nthawi yozula chimene chinabzalidwa.+ 3 Nthawi yakupha+ ndi nthawi yochiritsa.+ Nthawi yogumula ndi nthawi yomanga.+ 4 Nthawi yolira+ ndi nthawi yoseka.+ Nthawi yolira mofuula+ ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.+ 5 Nthawi yotaya miyala+ ndi nthawi younjika miyala pamodzi.+ Nthawi yokumbatirana+ ndi nthawi yosakumbatirana.+ 6 Nthawi yofunafuna+ ndi nthawi yovomereza kuti chinthu chatayika. Nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.+ 7 Nthawi yong’amba+ ndi nthawi yosoka.+ Nthawi yokhala chete+ ndi nthawi yolankhula.+ 8 Nthawi ya chikondi ndi nthawi ya chidani ndi munthu.+ Nthawi yankhondo+ ndi nthawi yamtendere.+ 9 Kodi munthu wogwira ntchito mwakhama adzapeza phindu lanji pa ntchito yakeyo?+

10 Ndaona ntchito imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira.+ 11 Chilichonse iye anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake.+ Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale+ kuti ntchito imene Mulungu woona wagwira, iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.+ 12 Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso azichita zabwino pamene ali ndi moyo,+ 13 komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+

14 Ndazindikira kuti zonse zimene Mulungu woona amapanga zimakhala mpaka kalekale.+ Palibe choti n’kuwonjezerapo kapena choti n’kuchotsapo.+ Mulungu woona ndi amene wapanga zimenezi,+ kuti anthu azimuopa.+

15 Zimene zilipo zinalipo kale, ndipo zimene zidzachitike zinachitikapo kale.+ Mulungu woona+ amafunafuna kuchitira zabwino anthu amene akuzunzidwa.+

16 Ine ndaonanso padziko lapansi pano kuti pamene panayenera kukhala chilungamo panali zoipa, ndipo pamene panayenera kuchitika zachilungamo panachitika zoipa.+ 17 Ine ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Mulungu woona adzaweruza munthu wolungama ndi munthu woipa,+ pakuti iye ali ndi nthawi yochitira chinthu chilichonse ndiponso yokhudza ntchito iliyonse.”+

18 Ineyo ndinanena mumtima mwanga kuti Mulungu woona adzasankhula ana a anthu. Zimenezi zidzawasonyeza kuti iwo ndi ofanana ndi zinyama.+ 19 Pakuti ana a anthu ali ndi mapeto, ndipo zinyamanso zili ndi mapeto. Mapeto a zonsezi ndi ofanana.+ Nyama imafa ndipo munthunso amafa.+ Mzimu wa zonsezi ndi umodzi,+ moti munthu saposa nyama, pakuti zonse n’zachabechabe. 20 Zonse zimapita kumalo amodzi.+ Zonse zinachokera kufumbi+ ndipo zonse zimabwerera kufumbi.+ 21 Ndani akudziwa ngati mzimu* wa ana a anthu umakwera m’mwamba, ndiponso ngati mzimu wa zinyama umatsika pansi?+ 22 Ine ndaona kuti palibe chabwino kuposa kuti munthu asangalale ndi ntchito yake,+ pakuti imeneyo ndi mphoto yake, popeza palibe amene adzam’bweretse kuti adzaone zimene zizidzachitika iye atafa.+

4 Ine ndinaganiziranso kuponderezana+ konse kumene kukuchitika padziko lapansi pano, ndipo ndinaona misozi ya anthu amene akuponderezedwa,+ koma panalibe wowatonthoza.+ M’manja mwa oponderezawo munali mphamvu, moti oponderezedwawo analibe wowatonthoza. 2 Ndinazindikira kuti anthu amene anafa kale ali bwino kuposa anthu amene ali moyo.+ 3 Koma amene ali bwino kuposa onsewa ndi amene sanabadwe,+ amene sanaone ntchito yosautsa mtima imene ikuchitika padziko lapansi pano.+

4 Ineyo ndaona ntchito yonse imene anthu amaigwira mwakhama ndiponso imene amaigwira bwino,+ kuti imabweretsa mpikisano pakati pa anthu.*+ Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.

5 Wopusa amapinda manja+ ake ndipo amadziwononga yekha.+

6 Kupuma pang’ono* kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama* ndi kuthamangitsa mphepo.+

7 Ine ndinaganiziranso zachabechabe zochitika padziko lapansi pano: 8 Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake.+ Alibenso mwana kapena m’bale wake,+ koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Komanso maso ake sakhutira ndi chuma.+ Iye amafunsa kuti: “Kodi ntchito yovutayi ndikugwirira ndani n’kumadzimana zinthu zabwino?”+ Izinso n’zachabechabe ndiponso ndi ntchito yosautsa mtima.+

9 Awiri amaposa mmodzi,+ chifukwa amapeza mphoto yabwino pa ntchito yawo imene amaigwira mwakhama.+ 10 Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.+ Koma kodi zingakhale bwanji munthu mmodzi atagwa popanda wina woti am’dzutse?+

11 Komanso, anthu awiri akagona pamodzi, amamva kutentha. Koma kodi mmodzi yekha angamve bwanji kutentha?+ 12 Ngati wina angagonjetse munthu mmodzi, anthu awiri akhoza kulimbana naye.+ Ndipo chingwe chopotedwa ndi zingwe zitatu sichingaduke msanga.

13 Mwana wosauka koma wanzeru ali bwino+ kuposa mfumu yokalamba koma yopusa,+ imene sionanso kufunika kochenjezedwa.+ 14 Pakuti mwanayo amatuluka m’ndende n’kukhala mfumu,+ ngakhale kuti anabadwa ngati wosauka mu ufumuwo.+ 15 Ndaona anthu onse amoyo amene amayenda padziko lapansi pano. Ndaonanso mmene zimakhalira ndi mwana amene amalowa m’malo mwa mfumu.+ 16 Ngakhale kuti anthu amene anali kumbali yake anali ambiri,+ pambuyo pake sadzakhutira naye,+ pakuti zimenezinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.+

5 Samala mayendedwe+ ako ukapita kunyumba ya Mulungu woona. Ukapita kumeneko uzikamvetsera,+ osati uzikapereka nsembe monga mmene amachitira anthu opusa,+ pakuti iwo sadziwa kuti akuchita zoipa.+

2 Usamapupulume kulankhula, ndipo mtima wako+ usamafulumire kulankhula pamaso pa Mulungu woona,+ chifukwa Mulungu woona ali kumwamba+ koma iwe uli padziko lapansi. N’chifukwa chake suyenera kulankhula zambiri.+ 3 Pakuti maloto amabwera chifukwa chochuluka zochita,+ ndipo kuchuluka kwa mawu kumachititsa munthu kulankhula zinthu zopusa.+ 4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+ 5 Kuli bwino kuti usalonjeze+ kusiyana ndi kulonjeza koma osakwaniritsa zimene walonjezazo.+ 6 Usalole kuti pakamwa pako pakuchimwitse,+ komanso usamanene kwa mngelo+ kuti unalakwitsa.+ Kodi Mulungu woona akwiyirenji chifukwa cha mawu ako n’kuwononga ntchito ya manja ako?+ 7 Chifukwa chochuluka zochita pamakhala maloto,+ zinthu zachabechabe, ndi mawu ochuluka. Koma uziopa Mulungu woona yekha.+

8 Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo+ zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo.+ Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo+ akuona,+ ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.

9 Komanso, phindu la dziko lapansi ndi la munthu aliyense,+ chifukwa ngakhale mfumu imadalira kuti munda wake ulimidwe, kuti ipindule ndi zokolola za kumundako.+

10 Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.+ Zimenezinso n’zachabechabe.+

11 Zinthu zabwino zikachuluka ozidya amachulukanso,+ ndipo kodi mwiniwake wa zinthuzo amapindula chiyani kuposa kumangoziyang’ana ndi maso ake?+

12 Wotumikira munthu wina amagona tulo tokoma+ ngakhale adye zochepa kapena zambiri. Koma zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.

13 Pali chinthu chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndaona padziko lapansi pano: Munthu kumangosunga chuma chake n’kudzapwetekedwa nacho.+ 14 Chumacho chimatha+ chifukwa cha zoipa zinazake zimene zachitika, kenako iye amabereka mwana wamwamuna pamene alibe chilichonse choti angapatse mwanayo ngati cholowa.+

15 Monga mmene munthu anabadwira kuchokera m’mimba mwa mayi ake, adzapitanso wamaliseche+ ngati mmene anabwerera, ndipo palibe chilichonse chimene adzatenge+ pa ntchito yake imene anaigwira mwakhama.

16 Palinso chinthu china chomvetsa chisoni kwambiri: Monga mmene munthu anabwerera, adzapitanso chimodzimodzi. Kodi pali phindu lanji kwa munthu amene amachita khama kugwirira ntchito mphepo?+ 17 Komanso, masiku onse a moyo wake amadya chakudya chake mu mdima ndi kusautsika mtima kwakukulu,+ amadwala, ndiponso amakhala ndi nkhawa.

18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso chokongola chimene ine ndaona, n’chakuti munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala, chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta+ imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku onse a moyo wake amene Mulungu woona wam’patsa. Pakuti imeneyo ndiyo mphoto yake. 19 Komanso, munthu aliyense amene Mulungu woona wam’patsa chuma ndiponso zinthu zambiri,+ ndiye kuti wamulola kuti adye kuchokera pa zinthuzo.+ Wamulolanso kuti alandire mphoto yake ndi kusangalala chifukwa cha ntchito yake imene amaigwira mwakhama.+ Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+ 20 Pakuti zowawa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukira kawirikawiri, chifukwa Mulungu woona akuchititsa kuti mtima wake uzisangalala.+

6 Pali zinthu zomvetsa chisoni zimene ndaona padziko lapansi pano, ndipo n’zofala pakati pa anthu: 2 Pali munthu amene Mulungu woona amam’patsa chuma, katundu, ndi ulemerero,+ ndiponso amene sasowa chilichonse chimene moyo wake umalakalaka,+ koma Mulungu woona samulola kudya zinthu zakezo,+ ndipo mlendo+ ndi amene amazidya. Zimenezi n’zachabechabe ndipo ndi nthenda yoipa. 3 Ngati munthu atabereka ana 100+ n’kukhala ndi moyo zaka zambirimbiri, masiku a moyo wake n’kukhala ochuluka,+ koma moyo wake osakhutira ndi zinthu zabwino,+ komanso osalowa m’manda,+ ndithu mwana amene anabadwa wakufa ali bwino kuposa iyeyu.+ 4 Pakuti mwanayu anangobadwira pachabe. Iye anapita mu mdima ndipo dzina lake lidzaphimbidwa ndi mdima.+ 5 Ngakhale dzuwa sanalione, kapena kulidziwa.+ Ameneyu ali ndi mpumulo kusiyana ndi woyamba uja.+ 6 Ngakhale munthu atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma sanasangalale ndi zabwino,+ kodi phindu lake n’chiyani? Pajatu aliyense amapita kumalo amodzi.+

7 Ntchito yonse imene anthu amaigwira mwakhama amagwirira pakamwa pawo,+ koma moyo wawo sukhuta. 8 Kodi munthu wanzeru amaposa bwanji munthu wopusa?+ Kodi munthu wovutika amapindula chiyani chifukwa chodziwa mmene angachitire zinthu ndi anthu? 9 Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.+ Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.+

10 Chilichonse chimene chinakhalapo chinapatsidwa kale dzina, ndipo zinadziwika kale kuti munthu ndi ndani.+ Iye sangathe kudziteteza pa mlandu wotsutsana ndi amene ali wamphamvu kuposa iyeyo.+

11 Chifukwa chakuti pali zambiri zoyambitsa zinthu zachabe,+ kodi munthu amapindula chiyani? 12 Ndani angadziwe zabwino zimene munthu angachite pa moyo wake,+ masiku onse a moyo wake wachabechabe, umene umakhala ngati mthunzi?+ Pakuti ndani angamuuze munthu zimene zidzachitike padziko lapansi pano iyeyo atafa?+

7 Mbiri yabwino imaposa mafuta onunkhira,+ ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa.+ 2 Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero,+ chifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Chotero munthu amene ali moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake. 3 Kuli bwino kumva chisoni kusiyana ndi kuseka,+ pakuti nkhope yachisoni imachititsa kuti mtima wa munthu ukhale wabwino.+ 4 Mtima wa anthu anzeru umakhala m’nyumba yamaliro,+ koma mtima wa anthu opusa umakhala m’nyumba yachisangalalo.+

5 Kuli bwino kumvetsera munthu wanzeru akamakudzudzula,+ kusiyana ndi kumvetsera nyimbo ya anthu opusa.+ 6 Pakuti kuseka kwa anthu opusa+ kumamveka ngati kuthetheka kwa minga zomwe zikuyaka pansi pa mphika. Izinso n’zachabechabe. 7 Kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mphatso+ ikhoza kuwononga mtima wa munthu.+

8 Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake,+ ndipo munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza.+ 9 Usamafulumire kukwiya mumtima mwako,+ pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.+

10 Usanene kuti: “N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?”+ Pakuti si nzeru+ kufunsa funso lotere.

11 Munthu wanzeru akalandira cholowa zimakhala bwino, ndipo nzeru zimapindulitsa anthu amene ali padziko lapansi.+ 12 Pakuti nzeru zimateteza+ monga mmene ndalama zimatetezera,+ koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi wakuti nzeru zimasunga moyo wa eni nzeruzo.+

13 Taona ntchito+ ya Mulungu woona, pakuti ndani angathe kuwongola zinthu zimene iye anazikhotetsa?+ 14 Pa tsiku labwino ukhale munthu wabwino,+ ndipo pa tsiku latsoka uzindikire kuti Mulungu woona anapanga masiku onsewa mofanana,+ ndi cholinga chakuti anthu asadziwe chilichonse chimene chidzachitike pambuyo pawo.+

15 Ndaona zinthu zonse m’masiku anga opanda pake.+ Pali munthu wolungama amene amawonongeka akuchita zolungama,+ ndipo pali munthu woipa amene amakhala ndi moyo wautali akuchitabe zoipa.+

16 Usakhale wolungama mopitirira muyezo+ kapena kudzionetsera kuti ndiwe wanzeru kwambiri,+ kuopera kuti ungadzibweretsere chiwonongeko.+ 17 Usakhale woipa mopitirira muyezo,+ komanso usakhale wopusa.+ Uferenji mwamsanga?+ 18 Ndi bwino kuti usunge malangizo oyambawo, ndipo usasiye malangizo achiwiriwo.+ Pakuti munthu amene amaopa Mulungu adzamvera malangizo onsewa.+

19 Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wamphamvu kuposa atsogoleri 10 amphamvu amene ali mumzinda.+ 20 Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.+

21 Komanso usamaganizire kwambiri mawu onse amene anthu amalankhula,+ kuti ungamve wantchito wako akukunenera zoipa.+ 22 Pakuti mtima wako ukudziwa bwino kuti ngakhale iweyo wanenerapo anthu ena zoipa kambirimbiri.+

23 Zonsezi ndinazifufuza mwanzeru ndipo ndinati: “Ndidzakhala wanzeru.” Koma nzeruzo zinatalikirana nane.+ 24 Zimene zinachitika kale n’zapatali ndiponso n’zozama kwambiri. Ndani angazimvetse?+ 25 Ineyo ndinaganiziranso mumtima mwanga+ kuti ndidziwe, ndifufuze, ndiponso ndifunefune nzeru.+ Ndinafunanso kudziwa zimene zimayambitsa zinthu,+ ndiponso kudziwa kuipa kwa kupusa ndi uchitsiru wa misala.+ 26 Ndipo izi n’zimene ndinapeza: Mkazi amene ali ngati ukonde wosakira nyama, amene mtima wake uli ngati khoka, amene manja ake ali ngati unyolo,+ ndi wowawa kuposa imfa.+ Munthu amakhala wabwino pamaso pa Mulungu woona akapulumuka kwa mkaziyo, koma amachimwa akagwidwa naye.+

27 Wosonkhanitsa+ anati: “Taona zimene ndapeza. Ndafufuza chinthu chimodzichimodzi kuti ndidziwe tanthauzo la zonsezi,+ 28 limene ndakhala ndikulifunafuna koma osalipeza. Pa anthu 1,000, ndapezapo mwamuna mmodzi yekha wowongoka mtima,+ koma pa anthu onsewa sindinapezepo mkazi wowongoka mtima.+ 29 Zimene ndapeza n’zakuti, Mulungu woona anapanga anthu owongoka mtima,+ koma anthuwo asankha njira zina zambirimbiri.”+

8 Ndani angafanane ndi munthu wanzeru?+ Ndipo ndani amadziwa kumasulira zinthu?+ Nzeru za munthu zimachititsa nkhope yake kuwala ndipo ngakhale nkhope yake yokwiya imasintha n’kumaoneka bwino.+

2 Ndikunena kuti: “Sunga lamulo la mfumu.+ Chita zimenezi polemekeza lumbiro la Mulungu.+ 3 Usafulumire kuchoka pamaso pake,+ ndipo usayambe kuchita zoipa.+ Pakuti mfumuyo idzachita zonse zimene ikufuna kuchita,+ 4 chifukwa mawu a mfumu ali ndi mphamvu yolamulira,+ ndipo ndani angaifunse kuti: ‘Kodi mukuchita chiyani?’”

5 Wosunga malamulo sadzakumana ndi tsoka lililonse,+ ndipo mtima wanzeru udzadziwa nthawi ndi chiweruzo.+ 6 Chochitika chilichonse chili ndi nthawi yake ndi chiweruzo chake,+ chifukwa mavuto a anthu ndi ambiri.+ 7 Pakuti palibe akudziwa zimene zidzachitike,+ popeza ndani angamuuze mmene zidzachitikire?

8 Palibe munthu amene ali ndi mphamvu pa mzimu kuti auletse mzimuwo.+ Palibenso amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa.+ Palibe amene samenya nawo nkhondo,+ ndipo kuchita zoipa sikudzapulumutsa amene amachita zoipawo.+

9 Zonsezi ndaziona ndipo mtima wanga unaganizira za ntchito iliyonse imene yachitidwa padziko lapansi pano, pa nthawi imene munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.+ 10 Koma ngakhale zili choncho, ndaona anthu oipa akuikidwa m’manda.+ Ndaonanso mmene iwo anabwerera ndi mmene anachokera pamalo oyera,+ n’kuiwalika mumzinda umene anali kuchitiramo zoipazo.+ Izinso n’zachabechabe.

11 Popeza anthu ochita zoipa sanalangidwe msanga,+ n’chifukwa chake mtima wa ana a anthu wakhazikika pa kuchita zoipa.+ 12 Ngakhale woipa atachita zoipa+ maulendo 100 n’kukhala ndi moyo wautali akuchitabe zofuna zake, ine ndikudziwa kuti anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino,+ chifukwa chakuti anali kumuopa.+ 13 Koma woipayo sizidzamuyendera bwino n’komwe,+ ndiponso sadzachulukitsa masiku ake amene ali ngati mthunzi,+ chifukwa saopa Mulungu.+

14 Pali chinthu china chachabe chimene chimachitika padziko lapansi: Pali anthu olungama amene amakumana ndi zinthu zimene amayenera kukumana nazo anthu oipa,+ ndiponso pali anthu oipa amene amakumana ndi zinthu zimene amayenera kukumana nazo anthu olungama.+ Ndinanena kuti zimenezinso n’zachabechabe.

15 Ineyo ndinatamanda kusangalala,+ chifukwa palibe chabwino chimene anthu angachite padziko lapansi pano kuposa kudya, kumwa ndi kusangalala, pamene akugwira ntchito mwakhama masiku onse a moyo wawo,+ amene Mulungu woona wawapatsa padziko lapansi pano.+ 16 Mogwirizana ndi zimenezi ndinatsimikiza mumtima mwanga+ kuti ndidziwe nzeru ndiponso ndione ntchito imene ikuchitika padziko lapansi,+ chifukwa alipo amene sagona tulo usana ndi usiku.+

17 Ndinaona ntchito yonse ya Mulungu woona,+ ndipo ndinaona kuti anthu amalephera kudziwa ntchito imene yachitika padziko lapansi pano.+ Kaya anthu ayesetse bwanji kuifufuza, safika poidziwa.+ Ngakhale atanena kuti ali ndi nzeru zokwanira zodziwira zinthu,+ sangathe kuidziwa.+

9 Ine ndinafuna kumvetsetsa ndi kuganizira mozama zinthu zonsezi:+ Anthu olungama ndiponso anthu anzeru limodzi ndi ntchito zawo ali m’dzanja la Mulungu woona.+ Anthu sadziwa za chikondi kapena chidani chimene chinalipo iwo asanakhalepo.+ 2 Zimene zimachitikira anthu onse n’zofanana.+ Pali mapeto amodzi+ kwa munthu wolungama+ ndi woipa,+ kwa munthu wabwino, woyera, ndi wodetsedwa, ndiponso kwa munthu amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe. Munthu wabwino n’chimodzimodzi ndi munthu wochimwa.+ Munthu amene amalumbira mosaganizira bwino n’chimodzimodzi ndi amene amaopa kulumbira.+ 3 Chimene chimamvetsa chisoni pa zinthu zonse zimene zimachitika padziko lapansi pano n’chakuti, popeza mapeto a anthu onse ndi amodzi,+ mtima wa ana a anthu ndi wodzazanso ndi zoipa.+ Mumtima mwawo mumakhala misala+ pa nthawi imene ali ndi moyo ndipo pamapeto pake, iwo amapita kwa akufa.+

4 Aliyense amene ali pakati pa anthu amoyo ali ndi chiyembekezo, chifukwa galu wamoyo+ ali bwino kuposa mkango wakufa.+ 5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse.+ Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.+ 6 Komanso chikondi chawo, chidani chawo ndiponso nsanje yawo zatha kale,+ ndipo alibenso gawo mpaka kalekale pa chilichonse chimene chikuchitika padziko lapansi pano.+

7 Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala,+ chifukwa Mulungu woona wakondwera kale ndi ntchito zako.+ 8 Nthawi zonse zovala zako zizikhala zoyera,+ ndipo pamutu pako pasamasowe mafuta.+ 9 Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi wako amene umamukonda+ masiku onse a moyo wako wachabechabe, amene Mulungu wakupatsa padziko lapansi pano. Usangalale masiku ako onse achabechabe, pakuti imeneyo ndiyo mphoto yako pamoyo,+ ndi pa ntchito yovuta imene ukuigwira mwakhama padziko lapansi pano. 10 Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse,+ pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu,+ kapena nzeru,+ ku Manda*+ kumene ukupitako.+

11 Nditaganizanso ndinaona kuti padziko lapansi pano anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano,+ amphamvu sapambana pankhondo,+ anzeru sapeza chakudya,+ omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma,+ ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa,+ chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.+ 12 Pakuti munthu+ nayenso sadziwa nthawi yake.+ Monga nsomba zimene zagwidwa mu ukonde wakupha,+ ndi mbalame zimene zakodwa mumsampha,+ ana a anthu nawonso amakodwa pa nthawi yatsoka,+ nthawiyo ikawafikira mwadzidzidzi.+

13 Padziko lapansi pano ndinaonapo nzeru izi, zimene zinali zogometsa kwa ine: 14 Panali mzinda winawake waung’ono ndipo mumzindamo munali amuna ochepa. Kenako kunabwera mfumu yamphamvu ndipo inazungulira mzindawo, n’kuunjika milu ikuluikulu yadothi yoti imenyerepo nkhondo.+ 15 Mumzindawo munali munthu wina wosauka koma wanzeru, amene anapulumutsa mzindawo chifukwa cha nzeru zake.+ Koma kenako palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo.+ 16 Choncho ineyo ndinati: “Nzeru n’zabwino kuposa mphamvu,+ koma nzeru za munthu wosauka zimanyozedwa ndipo anthu samvera mawu ake.”+

17 Mawu otsitsa a anthu anzeru amamveka kwambiri+ kuposa kukuwa kwa munthu amene akulamulira pakati pa anthu opusa.+

18 Ndi bwino kukhala ndi nzeru kuposa kukhala ndi zida zomenyera nkhondo, ndipo wochimwa mmodzi yekha akhoza kuwononga zabwino zochuluka.+

10 Ntchentche zakufa n’zimene zimachititsa mafuta onunkhira oyengedwa bwino+ kuwola ndi kuyamba kununkha. Momwemonso uchitsiru pang’ono umawononga mbiri ya munthu amene akulemekezedwa chifukwa cha nzeru ndi ulemerero wake.+

2 Mtima wa munthu wanzeru uli kudzanja lake lamanja,+ koma mtima wa munthu wopusa uli kudzanja lake lamanzere.+ 3 Komanso, m’njira iliyonse imene munthu wopusa amayenda,+ mtima wake umakhala wopanda nzeru, ndipo amauza aliyense kuti ndi wopusa.+

4 Mzimu wa mtsogoleri ukakuukira, usachoke pamalo ako,+ chifukwa kudekha kumachepetsa machimo aakulu.+

5 Pali chinachake chomvetsa chisoni chimene ine ndaona padziko lapansi pano, cholakwa+ chimene amachita wolamulira:+ 6 Zitsiru zaikidwa pa maudindo ambiri akuluakulu,+ koma anthu oyenerera amangokhala pamalo otsika.

7 Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi,* koma akalonga akuyenda pansi ngati antchito.+

8 Amene akukumba dzenje adzagweramo,+ ndipo amene akugumula mpanda wamiyala njoka idzamuluma.+

9 Amene akuphwanya miyala, adzadzipweteka nayo, ndipo amene akuwaza nkhuni aziwaza mosamala.+

10 Ngati nkhwangwa yabuntha ndipo munthu sanainole,+ adzawononga mphamvu zake pachabe. Choncho kugwiritsa ntchito bwino nzeru kumapindulitsa.+

11 Njoka ikaluma munthu asanaiimbire nyimbo kuti aiseweretse,+ ndiye kuti palibe phindu kwa munthu woimba ndi lilime lakeyo.

12 Mawu a m’kamwa mwa munthu wanzeru amakhala osangalatsa,+ koma milomo ya munthu wopusa imamuwononga.+ 13 Chiyambi cha mawu a m’kamwa mwake ndi uchitsiru,+ ndipo mapeto a mawu a m’kamwa mwake ndi misala yomvetsa chisoni. 14 Ndipo chitsiru chimalankhula mawu ambiri.+

Munthu sadziwa chimene chidzachitike, ndipo ndani angamuuze zimene zidzachitike iye atafa?+

15 Ntchito imene opusa amagwira mwakhama imawatopetsa,+ chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe amene akudziwa njira yopitira mumzinda.+

16 Dziko iwe, kodi zidzakuthera bwanji ngati mfumu yako ili kamnyamata,+ ndipo akalonga ako amangokhalira kudya ngakhale m’mawa? 17 Dziko iwe, ndiwe wodala ngati mfumu yako ili mwana wochokera ku banja lachifumu, ndipo akalonga ako amadya pa nthawi yake kuti akhale amphamvu, osati kumangomwa mopitirira muyezo.+

18 Chifukwa cha ulesi waukulu denga* limaloshoka, ndipo chifukwa cha kuchita manja lende nyumba imadontha.+

19 Chakudya chimachititsa antchito kuseka, ndipo vinyo amachititsa moyo kusangalala,+ koma ndalama zimathandiza pa zinthu zonse.+

20 Ngakhale m’chipinda chako, usanenere mfumu zoipa,+ ndipo m’zipinda zimene umagona usanenere zoipa aliyense wolemera,+ chifukwa cholengedwa chouluka chikanena mawu ako ndipo chinachake chokhala ndi mapiko chikaulula zimene wanena.+

11 Tumiza mkate wako+ pamadzi,+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+ 2 Pereka gawo la zinthu zimene uli nazo kwa anthu 7, ngakhale 8,+ chifukwa sukudziwa tsoka limene lidzagwe padziko lapansi.+

3 Mitambo ikadzaza madzi, imakhuthulira mvula yochuluka padziko lapansi,+ ndipo mtengo+ ukagwera kum’mwera kapena kumpoto, pamene wagwerapo udzakhala pomwepo.

4 Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.+

5 Monga momwe sudziwira mmene mzimu umagwirira ntchito m’thupi la mwana amene ali m’mimba mwa mayi ake,+ momwemonso sudziwa ntchito ya Mulungu woona, amene amachita zinthu zonse.+

6 Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo,+ chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino,+ kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.

7 Kuwala n’kokoma ndipo ndi bwino kuti maso aone dzuwa.+ 8 Ngakhale munthu atakhala ndi moyo zaka zambiri, m’zaka zonsezo azisangalala.+ Iye akumbukire masiku a mdima,+ ngakhale atakhala ambiri. Tsiku lililonse limene likubwera n’lachabechabe.+

9 Mnyamatawe, sangalala+ ndi unyamata wako, ndipo mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako. Yenda m’njira za mtima wako ndiponso motsatira zimene maso ako akuona.+ Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza chifukwa cha zonsezi.+ 10 Choncho chotsa zosautsa mumtima mwako ndipo teteza thupi lako ku tsoka,+ chifukwa unyamata ndiponso pachimake pa moyo n’zachabechabe.+

12 Kumbukira Mlengi wako Wamkulu+ masiku a unyamata wako,+ asanafike masiku oipa+ komanso zisanafike zaka zimene udzati: “Moyo sukundisangalatsa.”+ 2 Uchite zimenezi kuwala kwa dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi kusanazime,+ ndiponso mitambo isanabwerere kuti igwetse mvula. 3 Pa nthawi imeneyo oyang’anira nyumba+ azidzanjenjemera, amuna amphamvu adzapindika,+ akazi opera ufa+ adzasiya kugwira ntchito chifukwa adzatsala ochepa, akazi oyang’ana pawindo+ azidzaona mdima, 4 zitseko zotulukira popita mumsewu zidzatsekedwa,+ phokoso la miyala yoperera ufa lidzayamba kumveka motsika,+ ndipo munthu azidzadzuka ndi kulira kwa mbalame, ndiponso ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu otsika.+ 5 Komanso uzidzaopa chimene chili pamwamba ndipo m’njira mudzakhala zoopsa. Mtengo wa amondi udzachita maluwa,+ chiwala chizidzayenda mochita kudzikoka ndipo zakudya sizidzakoma,* popeza munthu adzakhala akupita kunyumba yake yokhalitsa+ ndipo olira azidzazungulira mumsewu.+ 6 Umukumbukire, chingwe chasiliva chisanachotsedwe, mbale yagolide isanaphwanyidwe,+ mtsuko usanaphwanyike pakasupe, ndiponso wilo lotungira madzi pachitsime lisanathyoke. 7 Kenako fumbi lidzabwerera kunthaka+ kumene linali, ndipo mzimu*+ udzabwerera kwa Mulungu woona+ amene anaupereka.+

8 Wosonkhanitsa+ anati: “Zachabechabe! Zinthu zonse n’zachabechabe.”+

9 Kuwonjezera pa kukhala ndi nzeru,+ wosonkhanitsayo nthawi zonse anali kuphunzitsanso anthuwo kuti adziwe zinthu.+ Anali kusinkhasinkha ndi kufufuza zinthu mosamala,+ ndipo analemba miyambi yambiri m’ndondomeko yoyenera.+ 10 Wosonkhanitsayo anafufuza mawu okoma+ ndipo analemba mawu olondola a choonadi.+

11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ng’ombe pozitsogolera,+ ndipo anthu amene amadzipereka kusonkhanitsa mawu anzeru, ali ngati misomali yokhomerera kwambiri.+ Mawuwo aperekedwa ndi m’busa mmodzi.+ 12 Mwana wanga, ponena za chilichonse chowonjezera pa izi, ndikukuchenjeza kuti: Kupanga mabuku ambiri sikudzatha ndipo kuwawerenga kwambiri kumangotopetsa munthu.+

13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita. 14 Pakuti Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.+

M’Chiheberi, dzina la bukuli ndi Qo·heʹleth kutanthauza, “wosonkhanitsa, munthu amene amasonkhanitsa anthu pamodzi, kapena amene amaitanitsa msonkhano.”

Mawu ake enieni, “pansi pa dzuwa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “mitsinje yoyenda nthawi yozizira.”

Onani Zakumapeto 4.

Kapena kuti, “imachitika chifukwa cha mpikisano pakati pa anthu.”

Mawu ake enieni, “kupuma kodzaza dzanja limodzi.”

Mawu ake enieni, “ntchito yovuta yodzaza manja awiri.”

Onani Zakumapeto 5.

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”

Kapena kuti, “tsindwi.”

“Zakudya sizidzakoma.” Mawu ake enieni akufotokoza kuti chipatso cha mtundu winawake, chimene munthu amadya kuti zakudya ziyambirenso kumukomera, chaphulika.

Onani Zakumapeto 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena