Yesaya
1 Masomphenya+ amene Yesaya+ mwana wa Amozi anaona, okhudza Yuda ndi Yerusalemu m’masiku a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda:+
2 Imvani+ kumwamba inu, ndipo tchera khutu iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena kuti: “Ndalera ana ndi kuwakulitsa,+ koma iwo andipandukira.+ 3 Ng’ombe yamphongo imam’dziwa bwino munthu amene anaigula, ndipo bulu amadziwa chinthu chimene mbuye wake amam’dyetseramo. Koma Isiraeli sandidziwa,+ ndipo anthu anga sanachite zinthu mozindikira.”+
4 Tsoka kwa mtundu wochimwa,+ anthu olemedwa ndi zolakwa, mbewu yochita zoipa,+ ana obweretsa chiwonongeko.+ Iwo amusiya Yehova.+ Achitira Woyera wa Isiraeli zinthu zopanda ulemu,+ ndipo abwerera m’mbuyo.+ 5 Kodi mumenyedwanso pati+ mmene mukupitiriza kupandukamu?+ Mutu wanu uli ndi zilonda zokhazokha, ndipo mtima wanu wafooka.+ 6 Kuyambira kuphazi mpaka kumutu palibe pabwino.+ Thupi lanu lonse lili ndi mabala ndi zilonda, ndiponso lanyukanyuka. Palibe amene wafinya zilonda zanuzo kapena kuzimanga. Palibenso amene wazifewetsa ndi mafuta.+ 7 Dziko lanu lawonongedwa.+ Mizinda yanu yatenthedwa ndi moto,+ ndipo alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona.+ Chilichonse chawonongeka ngati mmene zimakhalira adani akalanda dziko.+ 8 Mwana wamkazi wa Ziyoni+ wasiyidwa ngati msasa m’munda wa mpesa, ngati chisimba* m’munda wa minkhaka, ndiponso ngati mzinda umene wazunguliridwa ndi adani.+ 9 Yehova wa makamu akanapanda kutisiyira anthu ochepa opulumuka,+ tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.+
10 Imvani mawu a Yehova,+ inu olamulira ankhanza+ a ku Sodomu.+ Mvetserani malamulo a Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora. 11 Yehova wanena kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine? Nsembe zopsereza zathunthu+ za nkhosa zamphongo+ ndiponso mafuta a nyama zodyetsedwa bwino zandikwana.+ Ine sindikusangalalanso+ ndi magazi+ a ana a ng’ombe amphongo, ana a nkhosa amphongo ndiponso a mbuzi zamphongo.+ 12 Inu mukamabwerabwera kuti mudzaone nkhope yanga,+ kodi ndani wakuuzani kuti muchite zimenezi, kuti muzipondaponda mabwalo a panyumba panga?+ 13 Musabweretsenso nsembe zina zaufa zopanda phindu.+ Zofukiza zanu ndikunyansidwa nazo.+ Mumasunga masiku okhala mwezi+ ndi sabata,+ ndipo mumaitanitsa misonkhano.+ Koma ine ndatopa kukuonani mukugwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga+ pamene mukuchita misonkhano yapadera. 14 Moyo wanga ukudana ndi masiku anu okhala mwezi ndi zikondwerero zanu.+ Zimenezi zasanduka katundu wolemera kwa ine,+ ndipo ndatopa kuzinyamula.+ 15 Mukatambasula manja anu,+ ndimakubisirani maso anga.+ Ngakhale mupereke mapemphero ambiri,+ ine sindimvetsera.+ Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.+ 16 Sambani,+ dziyeretseni.+ Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga.+ Lekani kuchita zoipa.+ 17 Phunzirani kuchita zabwino.+ Funafunani chilungamo.+ Dzudzulani munthu wopondereza ena.+ Weruzani mwachilungamo mwana wamasiye.*+ Thandizani mkazi wamasiye pa mlandu wake.”+
18 Yehova akuti, “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+ Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.+ Ngakhale atakhala ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje. 19 Mukakhala ndi mtima wofuna kundimvera, mudzadya zabwino za m’dziko lanu.+ 20 Koma mukakana+ n’kupanduka, mudzawonongedwa ndi lupanga, chifukwa pakamwa pa Yehova m’pamene panena zimenezi.”+
21 Taonani! Mzinda wokhulupirika uja+ wasanduka hule.+ Unali wodzaza ndi chilungamo+ ndipo zachilungamo zinali kukhala mwa iye,+ koma tsopano muli zigawenga zopha anthu.+ 22 Siliva wako wasanduka zonyansa.*+ Mowa wako wa tirigu wasukuluka ndi madzi.+ 23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+
24 Choncho mawu a Ambuye woona, Yehova wa makamu, Wamphamvu wa Isiraeli,+ ndi akuti: “Eya! Ndidzibweretsera mpumulo pochotsa adani anga ndipo ndibwezera+ odana nane.+ 25 Ndidzakutembenuzirani dzanja langa. Ndidzasungunula zonyansa zanu zonse, ndipo ndidzachotsa nyansi zanu zonse.+ 26 Ndidzakubweretseraninso oweruza ngati pa chiyambi paja, ndi aphungu ngati poyamba paja.+ Pambuyo pa zimenezi mudzatchedwa Mzinda Wachilungamo ndi Mzinda Wokhulupirika.+ 27 Ziyoni adzapulumutsidwa+ ndi chilungamo ndipo anthu ake amene adzabwerere, adzapulumutsidwanso ndi chilungamo.+ 28 Kuwonongeka kwa opanduka ndi kwa ochimwa kudzachitikira limodzi,+ ndipo anthu omusiya Yehova adzatha.+ 29 Pakuti anthu adzachita manyazi ndi mitengo ikuluikulu imene inu munali kuilakalaka,+ ndipo mudzagwetsa nkhope zanu chifukwa cha minda imene mwasankha.+ 30 Pakuti mudzakhala ngati mtengo waukulu umene masamba ake akufota+ ndiponso ngati munda umene ulibe madzi. 31 Munthu wamphamvu adzakhala ngati chingwe chabwazi,+ ndipo ntchito yake idzakhala ngati kamoto kakang’ono. Zonsezi zidzayakira limodzi popanda wozizimitsa.”+
2 Zinthu zimene Yesaya mwana wa Amozi anaona zokhudza Yuda ndi Yerusalemu:+ 2 M’masiku otsiriza,+ phiri la nyumba+ ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri,+ ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono.+ Mitundu yonse idzakhamukira kumeneko.+ 3 Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: “Bwerani+ anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.”+ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mawu a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.+ 4 Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza mitundu yambiri ya anthu.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+
5 Inu amuna a m’nyumba ya Yakobo, bwerani tidzayende m’kuwala kwa Yehova.+
6 Pakuti mwawanyanyala anthu anu, nyumba ya Yakobo.+ Iwo adzaza ndi zinthu zochokera Kum’mawa.+ Akuchita zamatsenga+ ngati Afilisiti ndiponso ali ndi ana ambiri a alendo.+ 7 Dziko lawo ladzaza ndi siliva ndi golide, ndipo ali ndi chuma chopanda malire.+ Dziko lawo ladzaza ndi mahatchi,* ndipo ali ndi magaleta* osawerengeka.+ 8 Dziko lawo ladzaza ndi milungu yopanda phindu.+ Iwo amagwadira ntchito ya manja awo. Amagwadira chinthu chimene zala zawo zapanga.+ 9 Anthu ochokera kufumbi anyozeka. Iwo atsika ndipo simungathe kuwakhululukira.+
10 Lowani muthanthwe ndipo dzibiseni m’fumbi chifukwa cha kuopsa kwa Yehova, ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake.+ 11 Maso odzikuza a munthu wochokera kufumbi adzatsika, ndipo anthu odzikweza adzawerama.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+ 12 Pakuti ilo ndi tsiku la Yehova wa makamu.+ Tsikulo lidzafikira aliyense wodzitukumula ndi wodzikweza. Lidzafikiranso aliyense wokwezeka kapena wotsika.+ 13 Lidzafikira mikungudza yonse ya ku Lebanoni+ yodzikweza ndi yokwezeka. Lidzafikiranso mitengo yonse ikuluikulu ya ku Basana.+ 14 Lidzafikira mapiri onse akuluakulu odzikweza ndi mapiri onse ang’onoang’ono okwezeka.+ 15 Lidzafikiranso nsanja iliyonse yaitali ndi khoma* lililonse lolimba kwambiri.+ 16 Lidzafikira zombo zonse za ku Tarisi,+ ndi ngalawa zonse zabwinozabwino. 17 Munthu wodzikuza wochokera kufumbi adzawerama ndipo anthu odzikweza adzatsitsidwa.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+
18 Milungu yopanda phindu idzatheratu.+ 19 Mulungu akadzaimirira kuti dziko lapansi linjenjemere, anthu adzalowa m’mapanga a m’matanthwe ndi m’mayenje a m’nthaka chifukwa cha kuopsa kwa Yehova,+ ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake.+ 20 M’tsiku limenelo, munthu wochokera kufumbi adzataya milungu yake yasiliva yopanda pake ndi milungu yake yagolide yopanda phindu, imene anthu anamupangira kuti aziigwadira. Adzaitayira kumene kumakhala aswiswiri* ndi mileme,+ 21 kuti iye abisale m’mayenje a m’matanthwe ndi m’ming’alu ya m’miyala ikuluikulu. Adzachita zimenezi chifukwa cha kuopsa kwa Yehova, ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake,+ Mulunguyo akadzaimirira kuti dziko lapansi linjenjemere. 22 Kuti zinthu zikuyendereni bwino, musadalire munthu wochokera kufumbi amene mpweya wake uli m’mphuno mwake,+ pakuti palibe chifukwa choti mum’ganizire iyeyo.+
3 Tamverani! Ambuye woona,+ Yehova wa makamu, akuchotsa mu Yerusalemu+ ndi mu Yuda zinthu zonse zofunika pa moyo. Akuchotsa mkate, madzi,+ 2 mwamuna wamphamvu, munthu wankhondo, woweruza, mneneri,+ wowombeza, mwamuna wachikulire,+ 3 mtsogoleri wa anthu 50,+ munthu wolemekezeka kwambiri, mlangizi, katswiri wa matsenga ndi munthu wodziwa kuseweretsa njoka.+ 4 Ndidzaika anyamata kuti akhale akalonga awo ndipo anthu ankhanza adzawalamulira.+ 5 Anthu azidzalamulirana mwankhanza, ndipo munthu azidzachitira nkhanza munthu mnzake.+ Mnyamata adzaukira nkhalamba,+ ndipo wonyozeka adzaukira wolemekezeka.+ 6 Aliyense adzagwira m’bale wake m’nyumba mwa bambo ake n’kumuuza kuti: “Iwe uli ndi nsalu. Choncho ukhale wolamulira+ wathu ndipo uzilamulira mulu wa bwinjawu.” 7 Iye adzakweza mawu ake m’tsiku limenelo n’kunena kuti: “Ine sindikufuna kukhala womanga zilonda ndipo m’nyumba mwanga mulibe mkate kapena nsalu. Musandiike kuti ndikhale wolamulira anthuwa.”
8 Yerusalemu wapunthwa ndipo Yuda wagwa,+ chifukwa lilime lawo ndiponso zochita zawo n’zotsutsana ndi Yehova.+ Iwo achita zinthu zomupandukira m’maso ake olemekezeka.+ 9 Maonekedwe a nkhope zawo akuwachitira umboni wotsutsana nawo,+ ndipo anthuwo akunena za tchimo lawo lofanana ndi la Sodomu.+ Iwo sanalibise. Tsoka kwa iwo, chifukwa adzibweretsera mavuto.+
10 Amuna inu, nenani kuti anthu olungama zidzawayendera bwino,+ chifukwa adzadya zipatso za zochita zawo.+ 11 Tsoka kwa anthu oipa! Iwo adzaona zoopsa, chifukwa zimene anachitira ena ndi manja awo, zidzawachitikira iwowo.+ 12 Amene amagawira anthu anga ntchito, akuwagwiritsa ntchito mwankhanza, ndipo akazi ndi amene akuwalamulira.+ Inu anthu anga, amene akukutsogolerani akukusocheretsani,+ ndipo asokoneza njira yanu.+
13 Yehova wakhala pamalo ake kuti afotokoze mlandu wake, ndipo waimirira kuti aweruze mitundu ya anthu.+ 14 Yehova adzaweruza achikulire pakati pa anthu ake ndi akalonga ake.+
“Inuyo mwatentha munda wa mpesa. Zinthu zimene zinabedwa kwa anthu ovutika zili m’nyumba zanu.+ 15 Kodi amuna inu mukutanthauza chiyani pophwanya anthu anga ndi kupera nkhope za anthu ovutika?”+ akutero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.
16 Yehova wati: “Ana aakazi a Ziyoni ndi odzikuza. Iwo amayenda atasolola makosi awo ndiponso amakopa amuna ndi maso awo. Amayenda modzigomera, ndipo akamayenda mapazi awo amachita phokoso chifukwa cha zokongoletsera zimene amavala m’mapazi.+ 17 Choncho Yehova adzachititsa zipere+ m’mutu mwa ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzayeretsa pamutu pawo.+ 18 M’tsiku limenelo Yehova adzachotsa zokongoletsera zawo zonse: zibangili za m’miyendo, zinthu zomanga kumutu, zodzikongoletsera zooneka ngati mwezi,+ 19 ndolo,* zibangili za m’manja, nsalu zofunda,+ 20 nsalu zovala kumutu, matcheni ovala kumiyendo, malamba a pachifuwa,+ zoikamo mafuta onunkhira,* zigoba zodzikongoletsera,+ 21 mphete zovala m’zala, mphete zovala pamphuno,+ 22 mikanjo yovala pa nthawi zapadera, malaya ovala pamwamba, mikanjo yabwino kwambiri, tizikwama, 23 magalasi oonera a m’manja,+ zovala zamkati, nduwira,*+ ndi nsalu zofunda zikuluzikulu.+
24 “Ndiyeno chidzachitike n’chakuti, m’malo mwa mafuta a basamu onunkhira+ padzangokhala fungo loipa, m’malo mwa lamba padzakhala chingwe, m’malo mwa tsitsi lokonzedwa bwino padzakhala mpala,+ m’malo mwa chovala chamtengo wapatali munthu adzavala chiguduli,*+ ndipo padzakhala chipsera*+ m’malo mwa kukongola. 25 Amuna ako adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu ako amphamvu adzaphedwa pa nkhondo.+ 26 Zipata zake zidzalira+ ndipo zidzamva chisoni. Iye adzatsala wopanda chilichonse. Adzakhala pansi, padothi penipeni.”+
4 M’tsiku limenelo, akazi 7 adzagwira mwamuna mmodzi+ n’kumuuza kuti: “Ife tizidya chakudya chathu ndipo tizivala zovala zathu. Inuyo mungotilola kuti tizitchedwa ndi dzina lanu kuti tichotse chitonzo chathu.”+
2 M’tsiku limenelo, chinthu chimene Yehova adzachiphukitse+ chidzakhala chokongoletsera ndi chaulemerero.+ Zipatso za m’dzikolo zidzakhala zonyaditsa+ ndi zokongola kwa Aisiraeli amene adzapulumuke.+ 3 Amene adzatsale mu Ziyoni ndiponso amene adzatsale mu Yerusalemu adzakhala oyera kwa iye.+ Amenewa adzakhala anthu onse amene analembedwa mayina kuti akhale ndi moyo mu Yerusalemu.+
4 Yehova, pogwiritsa ntchito mzimu wa chiweruzo ndi mzimu wa moto,+ adzatsuka nyansi za ana aakazi a Ziyoni,+ ndiponso adzatsuka+ mkati mwa Yerusalemu n’kuchotsamo magazi amene Yerusalemuyo anakhetsa.+ 5 Akadzatero, malo onse a paphiri la Ziyoni+ ndiponso malo onse a mu Yerusalemu ochitirapo misonkhano, Yehova adzawapangira mtambo ndi utsi kuti ziziwathandiza masana. Adzawapangiranso kuwala kwa moto walawilawi+ kuti kuziwathandiza usiku,+ ndipo pamwamba pa malo onse aulemererowo padzakhala chotchinga.+ 6 Padzakhala msasa kuti uzipereka mthunzi woteteza ku dzuwa masana,+ ndiponso kuti ukhale pothawirapo ndi pobisalirapo mphepo yamkuntho ndi mvula.+
5 Ndikufuna ndimuimbire nyimbo munthu amene ndimamukonda. Imeneyi ndi nyimbo yonena za munthu amene ndimamukonda, ndiponso munda wake wa mpesa.+ Wokondedwa wanga anali ndi munda wa mpesa pamalo achonde m’mbali mwa phiri. 2 Iye analima mundawo n’kuchotsamo miyala, kenako anabzalamo mphesa zofiira zabwino kwambiri. Anamanga nsanja pakati pa mundawo.+ Anasemamonso choponderamo mphesa.+ Iye anali kuyembekezera kuti mundawo ubereka mphesa zabwino,+ koma unabereka mphesa zam’tchire.+
3 “Tsopano inu anthu okhala mu Yerusalemu ndiponso inu amuna a mu Yuda, weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesa.+ 4 N’chiyaninso chimene ndingachite m’munda wanga wa mpesawu chimene sindinachitemo kale?+ Ine ndinali kuyembekezera kuti ubereka mphesa zabwino, koma n’chifukwa chiyani unabereka mphesa zam’tchire? 5 Tsopano amuna inu, ndikuuzani zimene ndichite ndi munda wanga wa mpesa: Ndichotsa zomera zimene zinali ngati mpanda wa mundawo,+ ndipo ndiutentha.+ Ndigumula mpanda wake wamiyala ndipo mundawo udzangokhala malo oti azipondapondapo.+ 6 Ndidzangousiya kuti uwonongeke.+ Sindidzatengulira mitengo yake ndipo sindidzaulimanso.+ M’mundamo mudzamera tchire ndi zitsamba zaminga,+ ndipo ndidzalamula mitambo kuti isagwetsere mvula pamundawo.+ 7 Ine ndine Yehova wa makamu ndipo Isiraeli ndi munda wanga wa mpesa.+ Amuna a ku Yuda ndiwo mitengo ya mpesa imene ndinali kuikonda.+ Ine ndinali kuyembekezera chilungamo+ koma ndinaona anthu akuphwanya malamulo. Ndinali kuyembekezera zolungama koma ndinaona anthu akulira.”+
8 Tsoka kwa anthu amene akuwonjezera nyumba zina panyumba zawo,+ ndiponso amene akuwonjezera minda ina kuminda yawo, mpaka malo onse kutha,+ ndipo amuna inu mwayamba kukhala nokhanokha m’dzikoli. 9 Ndamva Yehova wa makamu akulumbira kuti nyumba zambiri, ngakhale zitakhala zikuluzikulu ndiponso zabwino, zidzakhala chinthu chodabwitsa kwambiri ndipo zidzakhala zopanda wokhalamo.+ 10 Pakuti maekala 10*+ a munda wa mpesa adzatulutsa mtsuko*+ umodzi wokha wa vinyo, ndipo mbewu zokwana muyezo umodzi wa homeri* zidzatulutsa zokolola zokwana muyezo umodzi wokha wa efa.*+
11 Tsoka kwa anthu amene amadzuka m’mawa kuti akafunefune chakumwa choledzeretsa.+ Amene amakhala akumwabe mpaka madzulo kutada, moti vinyo amawaledzeretsa.+ 12 Pa zikondwerero zawo amaimbapo azeze, zoimbira za zingwe, maseche, ndi zitoliro ndipo amamwapo vinyo.+ Koma sayang’ana ntchito ya Yehova, ndipo ntchito ya manja ake saiona.+
13 Chotero anthu anga adzapita ku ukapolo kudziko lina chifukwa chosadziwa zinthu.+ Anthu awo olemekezeka adzakhala amuna anjala+ ndipo khamu lawo lidzakhala louma kukhosi ndi ludzu.+ 14 Choncho, Manda* akulitsa malo ake ndipo atsegula kwambiri pakamwa pake kupitirira malire.+ Anthu olemekezeka a mumzindawo, khamu lake, phokoso lake ndi chikondwerero chake zidzatsikira m’mandamo.+ 15 Munthu wochokera kufumbi adzawerama. Iye adzatsika, ndipo ngakhale maso a anthu okwezeka adzatsika.+ 16 Yehova wa makamu adzakwezeka kudzera m’chiweruzo,+ ndipo Mulungu woona, Woyera,+ adzadziyeretsa kudzera m’chilungamo.+ 17 Kumeneko, ana a nkhosa amphongo adzadyako msipu ngati kuti ali pamalo odyetserapo ziweto. M’mabwinja mmene kale munali nyama zodyetsedwa bwino, alendo adzadyeramo.+
18 Tsoka kwa amene amakoka zolakwa ndi zingwe zopanda choonadi, ndi amene amakoka machimo ngati akuwakoka ndi zingwe zokokera ngolo.+ 19 Tsoka kwa amene amanena kuti: “Ntchito yake ifulumire, ibwere mwamsanga kuti tiione. Cholinga cha Woyera wa Isiraeli chichitike kuti tichidziwe.”+
20 Tsoka kwa amene akunena kuti chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino,+ amene akuika mdima m’malo mwa kuwala ndi kuwala m’malo mwa mdima, amene akuika zowawa m’malo mwa zotsekemera,* ndi zotsekemera m’malo mwa zowawa.+
21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru komanso amadziyesa ochenjera.+
22 Tsoka kwa anthu amene ali eni ake omwa vinyo kwambiri, ndi kwa anthu amene ali akatswiri odziwa kusakaniza zakumwa zoledzeretsa.+ 23 Tsoka kwa anthu amene amanena kuti woipa ndi wolungama chifukwa cholandira chiphuphu,+ ndiponso kwa amene amanena kuti wolungama ndi wolakwa.+
24 Chotero monga momwe lawi la moto limanyeketsera mapesi+ komanso monga mmene udzu wouma umanyekera m’malawi a moto, muzu wawo udzawola n’kuyamba kununkha.+ Maluwa awo adzauma n’kuuluzika ngati fumbi, chifukwa akana malamulo a Yehova wa makamu+ ndipo anyoza mawu a Woyera wa Isiraeli.+ 25 N’chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake ndipo adzatambasula dzanja lake n’kuwapha.+ Mapiri adzanjenjemera+ ndipo mitembo yawo idzakhala ngati zinyalala m’misewu.+
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula. 26 Iye waikira chizindikiro mtundu waukulu wakutali.+ Wauimbira likhweru kumapeto kwa dziko lapansi.+ Ndipotu mtunduwo udzachita changu n’kubwera msangamsanga.+ 27 Pakati pawo palibe aliyense wotopa ndipo palibe amene akupunthwa. Palibe amene akuwodzera ndipo palibe amene akugona. Lamba wa m’chiuno mwawo sadzamasulidwa ndipo zingwe za nsapato zawo sizidzaduka. 28 Mivi yawo ndi yakuthwa ndipo mauta awo onse ndi okungika.+ Ziboda za mahatchi awo n’zolimba ngati mwala wa nsangalabwi.+ Mawilo a magaleta awo ali ngati mphepo yamkuntho.+ 29 Kubangula kwawo kuli ngati kwa mkango ndipo amabangula ngati mikango yamphamvu.+ Iwo adzabangula n’kugwira nyama. Adzainyamula bwinobwino ndipo sipadzakhala woipulumutsa.+ 30 Iwo adzabangulira nyamayo m’tsiku limenelo ngati mkokomo wa nyanja.+ Munthu adzayang’ana dzikolo n’kuona kuti muli mdima womvetsa chisoni.+ Ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mvula imene idzagwe m’dzikolo.
6 M’chaka chimene Mfumu Uziya inamwalira,+ ine ndinaona Yehova+ atakhala pampando wachifumu+ wolemekezeka umene unali pamalo okwezeka, ndipo zovala zake zinadzaza m’kachisi.+ 2 Pamwamba pake panali aserafi.+ Mserafi aliyense anali ndi mapiko 6. Mapiko awiri anaphimbira nkhope yake,+ awiri anaphimbira mapazi ake ndipo awiri anali kuulukira. 3 Aliyense anali kuuza mnzake kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu.+ Zonse zimene zili padziko lapansi zimasonyeza ulemerero wake.” 4 Chifukwa cha mawuwo, mafelemu a zitseko+ anayamba kunjenjemera ndipo pang’ono ndi pang’ono, m’nyumbamo munadzaza utsi.+
5 Ine ndinati: “Tsoka kwa ine! Popeza maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.+ Nditsikira kuli chete pakuti ndine munthu wa milomo yodetsedwa,+ ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.”+
6 Pamenepo mserafi mmodzi anaulukira kwa ine. M’manja mwake munali khala lamoto+ limene analitenga paguwa lansembe ndi chopanira.+ 7 Iye anakhudza pakamwa panga+ n’kunena kuti: “Taona! Khalali lakhudza milomo yako, chotero zolakwa zako zachoka ndipo machimo ako aphimbidwa.”+
8 Kenako ndinayamba kumva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?”+ Ine ndinayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”+ 9 Iye anapitiriza kunena kuti: “Pita ukauze anthu awa kuti, ‘Imvani mobwerezabwereza anthu inu, koma musamvetsetse. Onani mobwerezabwereza, koma musazindikire chilichonse.’+ 10 Ukachititse anthu awa kuumitsa mtima wawo,+ ndipo ukachititse makutu awo kuti asamamve.+ Ukamate maso awo kuti asamaone ndi maso awowo, ndiponso kuti asamamve ndi makutu awo, komanso kuti mtima wawo usamvetsetse zinthu, kuti angatembenuke n’kuchira.”+
11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+ 12 Mpaka Yehova atathamangitsira anthu kutali, ndiponso mpaka mbali yaikulu ya dzikolo itakhala bwinja.+ 13 M’dzikolo mudzakhalabe chakhumi+ ndipo chidzakhalanso chinthu chofunika kuchitentha ngati mtengo waukulu, ndiponso ngati chimtengo chachikulu, chimene chikadulidwa+ pamatsala chitsa.+ Mbewu yopatulika idzakhala chitsa chake.”+
7 Tsopano m’masiku a Ahazi mwana wa Yotamu mwana wa Uziya+ mfumu ya Yuda, Rezini+ mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anabwera ku Yerusalemu kudzachita nkhondo koma analephera kulanda mzindawo.+ 2 Ndiyeno kunyumba ya Davide kunapita uthenga wakuti: “Dziko la Siriya layamba kudalira dziko la Efuraimu.”+
Choncho mtima wa Ahazi ndi wa anthu ake unayamba kunjenjemera, ngati mmene mitengo ya m’nkhalango imagwederera ndi mphepo.+
3 Tsopano Yehova anauza Yesaya kuti: “Pita ukakumane ndi Ahazi. Upite ndi mwana wako Seari-yasubu.*+ Ukakumane ndi Ahaziyo pamapeto pa ngalande+ yochokera kudziwe lakumtunda, m’mphepete mwa msewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+ 4 Ukamuuze kuti, ‘Ganizira mofatsa zochita zako.+ Usatekeseke kapena kuchita mantha. Mtima wako usaope+ zikuni ziwiri zimene zikungofuka utsi, zomwe zatsala pang’ono kunyekeratu. Usaope mkwiyo waukulu wa Rezini mfumu ya Siriya ndiponso usaope mwana wa Remaliya,+ 5 popeza Siriya ndi Efuraimu ndiponso mwana wa Remaliya akukonzera zoipa ndipo anena kuti: 6 “Tiyeni tikamenyane ndi dziko la Yuda. Tikalisakaze, tikalilande ndipo tikaligonjetse. Tikaike mfumu ina kuti izilamulira dzikolo. Mfumu yake ikhale mwana wa Tabeeli.”+
7 “‘Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sizitheka ndipo sizichitika.+ 8 Pakuti mutu wa Siriya ndiwo Damasiko, ndipo mutu wa Damasiko ndiwo Rezini. Pakamatha zaka 65, Efuraimu adzakhala ataphwanyidwaphwanyidwa moti sadzakhalanso mtundu wa anthu.+ 9 Mutu wa Efuraimu ndiwo Samariya,+ ndipo mutu wa Samariya ndiwo mwana wa Remaliya.+ Anthu inu mukakhala opanda chikhulupiriro, simukhalitsa.”’”+
10 Yehova analankhulanso ndi Ahazi kuti: 11 “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako.+ Chikhoza kukhala chozama ngati Manda kapena chachitali ngati malo okwera.” 12 Koma Ahazi anati: “Sindipempha, ndipo sindimuyesa Yehova.”
13 Chotero mneneriyo anati: “Tamverani inu a nyumba ya Davide. Kodi mukuona ngati n’zazing’ono kuti muzitopetsa anthu, ndiponso kuti mutopetse Mulungu wanga?+ 14 Choncho Yehovayo akupatsani chizindikiro anthu inu: Tamverani! Mtsikana+ adzatenga pakati+ ndipo adzabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli. 15 Iye azidzadya mafuta a mkaka ndi uchi pofika nthawi imene adzadziwe kukana choipa ndi kusankha chabwino.+ 16 Mwanayo asanafike podziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino,+ nthaka ya mafumu awiri amene ukuchita nawo mantha ofika podwala nawowo, idzakhala itasiyidwiratu.+ 17 Yehova adzabweretsera iweyo,+ anthu ako, ndi nyumba ya bambo ako masiku amene sanakhaleponso kuyambira tsiku limene Efuraimu anapatukana ndi Yuda.+ Iye adzakubweretserani mfumu ya Asuri.+
18 “M’tsiku limenelo, Yehova adzaimbira likhweru ntchentche zimene zili kumalekezero a ngalande za mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo, ndi njuchi+ zimene zili m’dziko la Asuri.+ 19 Zinthu zimenezi zidzabwera zonse n’kutera m’zigwa* zokhala ndi maphompho, m’ming’alu ya m’matanthwe, patchire lonse lokhala ndi zitsamba zaminga, ndiponso pamalo onse omwetserapo ziweto.+
20 “M’tsiku limenelo, pogwiritsira ntchito lezala lobwereka la kuchigawo cha ku Mtsinje,*+ pogwiritsira ntchito mfumu ya Asuri,+ Yehova adzameta tsitsi la kumutu ndi tsitsi la m’mapazi, ndipo lezalalo lidzachotseratu ngakhale ndevu.+
21 “M’tsiku limenelo, munthu adzapulumutsa ng’ombe yaing’ono ndiponso nkhosa ziwiri.+ 22 Chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka, iye azidzadya mafuta a mkaka, popeza mafuta a mkaka ndi uchi+ n’zimene munthu aliyense wotsala m’dzikolo azidzadya.
23 “M’tsiku limenelo, pamalo alionse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000, yokwana ndalama zasiliva 1,000,+ padzakhala tchire la zitsamba zaminga ndi udzu.+ 24 Anthu azidzapita kumeneko atanyamula mivi ndi mauta,+ chifukwa m’dziko lonselo mudzamera tchire la zitsamba zaminga ndi udzu. 25 Kumapiri onse amene anthu anali kulambulako ndi makasu kuti achotse zomera zovutitsa, sadzapitakonso chifukwa choopa tchire la zitsamba zaminga ndi udzu. Malowo adzakhala odyetserako ng’ombe zamphongo ndi opondapondako nkhosa.”+
8 Yehova anandiuza kuti: “Tenga cholembapo chachikulu+ ndipo ulembepo ndi cholembera wamba, kuti: ‘Maheri-salala-hasi-bazi.’* 2 Ndikufuna mboni zokhulupirika kuti zindichitire umboni.+ Mbonizo zikhale wansembe Uriya+ ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.”
3 Kenako ndinakhala malo amodzi ndi mneneri wamkazi ndipo iye anatenga pakati. Pambuyo pake anabereka mwana wamwamuna.+ Tsopano Yehova anandiuza kuti: “Um’patse dzina lakuti Maheri-salala-hasi-bazi, 4 popeza mwanayo asanadziwe kuitana+ kuti, ‘Ababa!’ kapena ‘Amama!’ anthu adzanyamula chuma cha ku Damasiko ndi katundu wolandidwa ku Samariya n’kupita naye pamaso pa mfumu ya Asuri.”+
5 Yehova anandiuzanso kuti: 6 “Popeza anthu awa akana+ madzi a ku Silowa+ amene amayenda pang’onopang’ono, ndipo atengeka+ ndi Rezini ndiponso mwana wa Remaliya,+ 7 Yehova akuwabweretsera+ Mtsinje*+ wa madzi ambiri ndi amphamvu, womwe ndi mfumu ya Asuri+ ndi ulemerero wake wonse.+ Iyo idzadzaza timitsinje take tonse n’kusefukira mpaka m’mphepete mwa mitsinje yake yonse, 8 ndipo idzadutsa mu Yuda yense. Idzadutsa ngati madzi osefukira,+ ndipo idzafika mpaka m’khosi.+ Idzatambasula mapiko ake+ mpaka m’lifupi mwa dziko lako, iwe Emanueli.”+
9 Inu mitundu ya anthu, vulazani anthu, koma inuyo muphwanyidwaphwanyidwa. Inu nonse amene muli kumalekezero a dziko lapansi, tamverani.+ Nyamulani zida zankhondo+ koma muphwanyidwaphwanyidwa.+ Nyamulani zida zankhondo koma muphwanyidwaphwanyidwa. 10 Konzani zochita, koma zidzalephereka.+ Nenani zoti anthu achite, koma sizidzachitidwa, chifukwa Mulungu ali nafe.+ 11 Dzanja lamphamvu la Yehova linali pa ine, ndipo pofuna kuti andipatutse kuti ndisayende panjira ya anthu awa, iye anati: 12 “Anthu inu musamanene kuti: ‘Chiwembu!’ pa nkhani zonse zimene anthu awa amanena kuti: ‘Chiwembu!’+ Musamaope zimene iwo amaopa ndipo musamanjenjemere nazo.+ 13 Yehova wa makamu ndi amene muyenera kumuona kuti ndi woyera,+ ndipo iyeyo ndi amene muyenera kumuopa.+ Iye ndi amene ayenera kukuchititsani kunjenjemera.”+
14 Iye akhale ngati malo opatulika.+ Koma kwa nyumba zonse ziwiri za Isiraeli, iye akhale ngati mwala wopunthwitsa ndiponso ngati mwala wokhumudwitsa.+ Akhalenso ngati msampha ndi khwekhwe kwa anthu okhala mu Yerusalemu.+ 15 Anthu ambiri pakati pawo adzapunthwa n’kugwa ndi kuthyoka, ndipo adzakodwa n’kugwidwa.+
16 Kulunga umboni.+ Mata lamulo pakati pa ophunzira anga.+ 17 Ine ndiziyembekezera Yehova,+ amene wabisira nkhope yake nyumba ya Yakobo,+ ndipo ndithu ndiziyembekezera iyeyo.+
18 Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa+ tili ngati zizindikiro+ ndiponso ngati zozizwitsa mu Isiraeli, zochokera kwa Yehova wa makamu amene amakhala m’phiri la Ziyoni.+
19 Akakuuzani anthu inu kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu+ kapena kwa anthu amene ali ndi mzimu wolosera zam’tsogolo, omwe amalira ngati mbalame+ ndiponso amalankhula motsitsa mawu,” kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake?+ Kodi tizifunsira kwa anthu akufa kuti athandize anthu amoyo?+ 20 Funsirani kwa lamulo ndi umboni!+
Ndithu iwo azingonena zinthu zogwirizana ndi mawu amenewa,+ koma sadzaona kuwala kwa m’bandakucha.+ 21 Aliyense adzadutsa m’dzikolo akuzunzika ndiponso ali ndi njala.+ Chifukwa chakuti ali ndi njala ndiponso wakwiya, adzatukwana mfumu yake ndi Mulungu+ wake ndipo azidzayang’ana kumwamba. 22 Iye adzayang’ana padziko lapansi koma adzangoonapo kuzunzika, mdima,+ kuda, nthawi zovuta ndi zakuda bii, zopanda kuwala.+
9 Komabe mdima wake sudzakhala ngati wa pa nthawi imene dzikolo linali m’masautso, ngati kale pamene anthu ankanyoza dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali.+ Koma patsogolo pake anthu analilemekeza dzikolo,+ dera limene kuli njira ya m’mphepete mwa nyanja, m’chigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.+ 2 Anthu amene anali kuyenda mu mdima, aona kuwala kwakukulu.+ Anthu amene anali kukhala m’dziko la mdima wandiweyani,+ kuwala kwawawalira.+ 3 Mwachulukitsa mtundu,+ mwaupangitsa kusangalala kwambiri.+ Iwo asangalala pamaso panu ngati mmene amasangalalira pa nthawi yokolola,+ ngati anthu amene amasangalala akamagawana katundu amene alanda.+
4 Pakuti goli la katundu wawo,+ ndodo yomwe inali pamapewa awo, ndiponso ndodo ya amene anali kuwakusira ku ntchito,+ mwazithyolathyola ngati pa tsiku limene Amidiyani anagonjetsedwa.+ 5 Nsapato iliyonse ya munthu woyenda mwamgugu+ ndi chovala choviikidwa m’magazi, zakhala zoyenera kutenthedwa pamoto ngati nkhuni.+ 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+ 7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
8 Yehova anatumiza mawu otsutsana ndi Yakobo, ndipo mawuwo anafikira Isiraeli.+ 9 Mawu onsewa anthu adzawadziwa.+ Efuraimu ndi anthu okhala ku Samariya,+ adzawadziwa mawuwo chifukwa cha kudzikweza kwawo ndiponso chifukwa cha mwano wa mumtima mwawo. Pakuti iwo anena kuti:+ 10 “Nyumba za njerwa n’zimene zagwazi, koma ife timanga zina za miyala yosema.+ Mitengo ya mkuyu ndi imene yathyoledwayi, koma m’malo mwake ife tipezerapo mitengo ya mkungudza.”+ 11 Yehova adzakweza adani a Rezini pamwamba kwambiri kuti alimbane naye, ndipo adzalimbikitsa adani a Isiraeli.+ 12 Siriya adzachokera kum’mawa+ ndipo Afilisiti adzachokera kumadzulo.+ Iwo adzadya Isiraeli ndi pakamwa potsegula.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
13 Anthuwo sanabwerere kwa amene akuwamenya+ ndipo sanafunefune Yehova wa makamu,+ 14 chotero Yehova adzadula mutu+ ndi mchira+ wa Isiraeli. Adzadulanso mphukira ndi udzu* tsiku limodzi.+ 15 Munthu wokalamba ndi wolemekezeka kwambiri ndiye mutu,+ ndipo mneneri wopereka malangizo abodza ndiye mchira.+ 16 Amene akutsogolera anthuwa ndiwo amene akuwasocheretsa,+ ndipo amene akutsogoleredwawo ndiwo amene akusokonezedwa.+ 17 N’chifukwa chake Yehova sadzasangalalira ngakhale anyamata awo,+ ndipo sadzamvera chisoni ana awo amasiye* ndi akazi awo amasiye, pakuti onsewo ndi opanduka+ ndi ochita zoipa ndipo pakamwa paliponse pakulankhula zopanda nzeru. Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
18 Pakuti kuipa kwayaka ngati moto,+ ndipo kudzanyeketsa zitsamba zaminga ndi udzu.+ Kuipako kudzayaka m’zitsamba zowirira za m’nkhalango,+ ndipo utsi wa mitengoyo udzakwera m’mwamba kuti tolo!+ 19 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova wa makamu, dzikolo layaka moto ndipo anthu adzakhala ngati chakudya cha motowo.+ Palibe amene adzamvere chisoni aliyense, ngakhale m’bale wake.+ 20 Munthu adzacheka kumbali yake yakumanja, koma adzakhala ndi njala. Adzadya kumanzere kwake, koma sadzakhuta.+ Aliyense adzadya mnofu wa dzanja lake.+ 21 Manase adzadya Efuraimu ndipo Efuraimu adzadya Manase. Awiriwa adzaukira Yuda pamodzi.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
10 Tsoka kwa amene akukhazikitsa malamulo oipa,+ ndi kwa amene amangokhalira kulemba malamulo obweretsa mavuto kwa anthu. 2 Iwo amachita zimenezi n’cholinga choti asamvetsere mlandu wa anthu onyozeka ndiponso kuti anthu anga osautsika awalande chilungamo.+ Amateronso kuti atenge akazi amasiye ngati katundu wolanda ndiponso kuti atenge ana amasiye.*+ 3 Kodi anthu inu mudzatani pa tsiku limene adzatembenukire kwa inu+ ndi kukubweretserani chiwonongeko chochokera kutali?+ Mudzathawira kwa ndani kuti akuthandizeni+ ndipo ulemerero wanu mudzausiya kuti?+ 4 Palibe chimene mudzachite, koma mudzagwada pakati pa akaidi ndiponso muzidzagwa pakati pa anthu amene aphedwa.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
5 “Eya! Msuri+ ndiye ndodo ya mkwiyo wanga+ komanso chikwapu chosonyezera ukali wanga chimene chili m’dzanja lake. 6 Ndidzamutumiza kuti akalimbane ndi mtundu wopanduka,+ ndipo ndidzamulamula kuti akalimbane ndi anthu amene andikwiyitsa. Ndidzamuuza+ kuti akalande zinthu zambiri, akatenge katundu wambiri, ndiponso akapondeponde anthuwo ngati matope a mumsewu.+ 7 Ngakhale iye atakhala kuti si wotero, adzafunabe kuchita zimenezi. Ngakhale mtima wake utakhala kuti si wotero, adzakonza zoti achite zimenezi, chifukwa chakuti mumtima mwake amaganiza zowononga+ ndiponso zoti awonongeretu mitundu yambiri.+ 8 Pakuti iye adzanena kuti, ‘Kodi akalonga anga si mafumunso?+ 9 Kodi Kalino+ sali ngati Karikemisi?+ Kodi Hamati+ sali ngati Aripadi?+ Kodi Samariya+ sali ngati Damasiko?+ 10 Nthawi iliyonse imene dzanja langa lafikira maufumu olambira milungu yopanda phindu, omwe zifaniziro zawo zogoba n’zambiri kuposa zimene zili ku Yerusalemu ndi ku Samariya,+ 11 kodi sizidzachitika kuti monga momwe ndidzachitire kwa Samariya ndi kwa milungu yake yopanda phindu,+ ndi mmenenso ndidzachitire kwa Yerusalemu ndi kwa mafano ake?’+
12 “Yehova akadzatsiriza ntchito yake yonse m’phiri la Ziyoni ndi mu Yerusalemu, ndidzalanga mfumu ya Asuri chifukwa cha zipatso za mwano wa mumtima mwake ndiponso chifukwa cha kudzikuza kwa maso ake onyada.+ 13 Pakuti iye wanena kuti, ‘Ndi mphamvu za dzanja langa ndiponso ndi nzeru zanga, ndidzachitapo kanthu+ chifukwa ndine wodziwa zinthu. Ndidzachotsa malire a mitundu ya anthu,+ ndipo zinthu zimene anasunga ndidzazilanda.+ Monga munthu wamphamvu, ndidzagwetsa anthu okhala mmenemo.+ 14 Dzanja langa+ lidzafikira chuma+ cha mitundu ya anthu ngati likupisa m’chisa. Ngati mmene munthu amatengera mazira amene asiyidwa, ine ndidzatenga dziko lonse lapansi. Sipadzakhala aliyense wokupiza mapiko ake kapena wotsegula pakamwa pake, kapenanso wolira ngati mbalame.’”
15 Kodi nkhwangwa ingadzikuze kuposa munthu amene akuigwiritsa ntchito? Kapena kodi chochekera matabwa chingadzikweze kuposa munthu amene akuchigwiritsa ntchito? Kodi chikwapu chinganyamule munthu amene wachinyamula m’mwamba, ndiponso kodi ndodo inganyamule m’mwamba munthu amene si mtengo?+ 16 Chotero Ambuye woona, Yehova wa makamu azidzatumizira anthu ake* onenepa nthenda yowondetsa,+ ndipo pansi pa ulemerero wake pazidzangoyaka, ngati kuyaka kwa moto.+ 17 Kuwala kwa Isiraeli+ kudzasanduka moto+ ndipo Woyera wake adzasanduka lawi la moto.+ Iye adzayaka n’kunyeketsa udzu wake* ndi zitsamba zake zaminga+ pa tsiku limodzi. 18 Mulungu adzathetseratu ulemerero wa nkhalango yake* ndi wa munda wake wa zipatso,+ ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuonda.+ 19 Mitengo yotsala ya m’nkhalango mwake idzakhala yochepa kwambiri, moti kamnyamata kadzatha kulemba chiwerengero chake.+
20 M’tsiku limenelo, otsala a Isiraeli+ ndi opulumuka a nyumba ya Yakobo sadzadaliranso yemwe akuwamenya,+ koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova, Woyera wa Isiraeli.+ 21 Otsala ochepa adzabwerera.* Otsala a Yakobo adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.+ 22 Pakuti iwe Isiraeli, ngakhale anthu ako atakhala ngati mchenga wa kunyanja,+ otsala ochepa okha pakati pawo ndi amene adzabwerere.+ Chiwonongeko+ chimene Mulungu wakonzera anthu awa chidzabwera mwachilungamo ngati madzi osefukira,+ 23 chifukwa chakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, adzabweretsa chiwonongeko+ ndi chiweruzo chokhwima pakatikati pa dziko lonselo.+
24 Chotero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ wanena kuti: “Anthu anga amene mukukhala m’Ziyoni,+ musachite mantha chifukwa cha Msuri amene anali kukukwapulani ndi chikwapu+ ndiponso kukumenyani ndi ndodo, ngati mmene Iguputo anali kuchitira.+ 25 Pakuti pakangodutsa kanthawi kochepa, kudzudzulako+ kudzatha ndipo mkwiyo wanga udzawayakira, moti adzatha.+ 26 Yehova wa makamu adzam’kwapula ndi chikwapu+ ngati mmene anagonjetsera Midiyani pathanthwe la Orebi.+ Ndodo yake idzakhala panyanja+ ndipo adzaikweza m’mwamba ngati mmene anachitira ndi Iguputo.+
27 “M’tsiku limenelo, katundu wake adzachoka paphewa panu,+ ndipo goli lake lidzachoka m’khosi mwanu.+ Golilo lidzathyoledwa+ chifukwa cha mafuta.”
28 Iye waukira Ayati.+ Wadutsa ku Migironi. Waika katundu wake ku Mikimasi.+ 29 Wadutsa powolokera mtsinje. Usiku agona ku Geba.+ Rama+ wanjenjemera ndipo Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, wathawa. 30 Iwe mwana wamkazi wa Galimu,+ fuula kwambiri. Khala tcheru, iwe Laisa. Iwenso Anatoti wosautsika, khala tcheru!+ 31 Madimena wathawa. Anthu okhala ku Gebimu abisala. 32 Kukadali masana, iye aima ku Nobu.+ Ndi dzanja lake, iye akuopseza phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri limene pali Yerusalemu.+
33 Taonani! Ambuye woona, Yehova wa makamu, akuthyola nthambi ndipo zikugwa ndi chimkokomo.+ Nthambi zitalizitali zikudulidwa, ndipo zam’mwamba zatsitsidwa.+ 34 Iye wadula ndi nkhwangwa zitsamba zowirira za m’nkhalango, ndipo wamphamvu adzagwetsa mitengo ya ku Lebanoni.+
11 Nthambi+ idzatuluka pachitsa cha Jese,+ ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.+ 2 Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye,+ mzimu wanzeru,+ womvetsa zinthu,+ wolangiza, wamphamvu,+ wodziwa zinthu+ ndi woopa Yehova.+ 3 Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova.+
Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake.+ 4 Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka+ ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi. Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake,+ ndipo adzagwiritsa ntchito mzimu wa pakamwa pake kupha munthu woipa.+ 5 Chilungamo ndi kukhulupirika zidzakhala lamba wa m’chiuno mwake.+
6 Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa wamphongo kwa kanthawi,+ ndipo kambuku* adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi. Mwana wa ng’ombe, mkango wamphamvu+ ndi nyama yodyetsedwa bwino zidzakhala pamodzi,+ ndipo kamnyamata kakang’ono kadzakhala mtsogoleri wawo. 7 Ng’ombe ndi chimbalangondo zidzadyera pamodzi. Ana awo adzagona pansi pamodzi. Ngakhale mkango udzadya udzu ngati ng’ombe yamphongo.+ 8 Mwana woyamwa adzasewera pa una wa mamba,+ ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake kudzenje la njoka yapoizoni. 9 Sizidzavulazana+ kapena kuwonongana m’phiri langa lonse loyera,+ chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.+
10 M’tsiku limenelo,+ padzakhala muzu wa Jese+ womwe udzaimirire ngati chizindikiro kwa anthu.+ Ngakhale anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awatsogolere,+ ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.+
11 M’tsiku limenelo, Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri+ kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,+ ku Hamati ndi m’zilumba za m’nyanja.+ 12 Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu n’kusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumalekezero anayi a dziko lapansi.+
13 Nsanje ya Efuraimu idzatha,+ ndipo ngakhale anthu odana ndi Yuda adzaphedwa. Efuraimu sadzachitira nsanje Yuda ndiponso Yuda sadzadana ndi Efuraimu.+ 14 Iwo adzauluka paphewa la Afilisiti kumadzulo,+ ndipo onsewa pamodzi, adzalanda katundu wa ana aamuna a Kum’mawa.+ Adzatambasulira dzanja lawo pa Edomu ndi Mowabu,+ ndipo ana a Amoni adzawagonjera.+ 15 Yehova adzaphwetsa chigawo cha nyanja ya Iguputo,+ ndipo adzayendetsa dzanja lake moopseza Mtsinje*+ pogwiritsa ntchito mpweya wake wotentha. Adzamenya mtsinjewo pokwapula timitsinje take 7, ndipo adzachititsa anthu kuwolokapo nsapato zili kuphazi.+ 16 Padzakhala msewu waukulu+ wochokera kudziko la Asuri woti mudzadutse anthu ake amene adzatsale,+ monga mmene panalili msewu umodzi umene Aisiraeli anayendamo m’tsiku limene anatuluka m’dziko la Iguputo.
12 M’tsiku limenelo+ ndithu udzanena kuti: “Ndikukuthokozani inu Yehova pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu unabwerera pang’onopang’ono+ ndipo munanditonthoza.+ 2 Taonani! Mulungu ndiye chipulumutso changa.+ Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse,+ pakuti Ya* Yehova ndiye mphamvu zanga+ ndi nyonga zanga,+ ndipo iye wakhala chipulumutso changa.”+
3 Anthu inu ndithu mudzatunga madzi mosangalala pa akasupe a chipulumutso.+ 4 M’tsiku limenelo mudzanenadi kuti: “Yamikani Yehova anthu inu.+ Itanani pa dzina lake.+ Dziwitsani mitundu ya anthu zochita zake.+ Nenani kuti dzina lake n’lokwezeka.+ 5 Muimbireni nyimbo Yehova+ chifukwa wachita zopambana.+ Zimenezi zikulengezedwa m’dziko lonse lapansi.
6 “Fuula mwachisangalalo iwe mkazi wokhala mu Ziyoni, pakuti Woyera wa Isiraeli ndi wamkulu pakati pako.”+
13 Uwu ndi uthenga wokhudza Babulo,+ umene Yesaya mwana wa Amozi+ anaona m’masomphenya: 2 “Amuna inu, imikani chizindikiro+ paphiri la miyala yokhayokha. Afuulireni! Akodoleni ndi dzanja,+ kuti adzalowe pamakomo a anthu olemekezeka.+ 3 Ine ndapereka lamulo kwa opatulika anga.+ Ndaitananso anthu anga amphamvu oti asonyeze mkwiyo wanga.+ Amenewa ndi anthu anga okondwa kwambiri. 4 Tamverani! M’mapiri mukumveka phokoso la khamu la anthu, phokoso ngati la anthu ambiri.+ Tamverani! Kukumveka chisokonezo cha maufumu, cha mitundu imene yasonkhanitsidwa pamodzi.+ Yehova wa makamu akusonkhanitsira asilikali ku nkhondo.+ 5 Iwo akuchokera kudziko lakutali.+ Akuchokera kumalekezero a kumwamba. Yehova akubwera ndi zida za mkwiyo wake, kuti asakaze dziko lonse lapansi.+
6 “Fuulani, anthu inu,+ chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi.+ Lidzabwera ngati kuti Wamphamvuyonse akulanda zinthu.+ 7 N’chifukwa chake anthu onse adzataya mtima, ndipo mitima ya anthu onse idzasungunuka.+ 8 Anthu asokonezeka.+ Nsautso ndi zowawa za pobereka zawagwera. Iwo akumva zowawa ngati mkazi amene akubereka.+ Akuyang’anana modabwa. Nkhope zawo zafiira ndi mantha.+
9 “Taonani! Tsiku la Yehova likubwera. Tsikulo n’lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto. Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chodabwitsa,+ ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa a m’dzikolo.+ 10 Pakuti nyenyezi zakumwamba ndi magulu a nyenyezi a Kesili+ sizidzawala. Dzuwa lidzachita mdima potuluka, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake. 11 Nthaka ndidzaibwezera zoipa zake,+ ndipo anthu oipa ndidzawabwezera zolakwa zawo. Kunyada kwa anthu odzikuza ndidzakuthetsa, ndipo ndidzatsitsa olamulira ankhanza ndi odzikweza.+ 12 Ndidzachititsa kuti anthu azisowa kwambiri kuposa golide woyengedwa bwino,+ ndiponso ndidzachititsa kuti anthu ochokera kufumbi azisowa kwambiri kuposa golide wa ku Ofiri.+ 13 Chifukwa cha zimenezi, ndidzachititsa kuti kumwamba kugwedezeke+ ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera n’kuchoka m’malo mwake, chifukwa cha ukali wa Yehova wa makamu,+ pa tsiku limene mkwiyo wake udzayake.+ 14 Monga insa imene ikuthamangitsidwa ndiponso monga ziweto zopanda wozikusa,+ aliyense wa iwo adzatembenukira kwa anthu ake, ndipo aliyense wa iwo adzathawira kudziko lake.+ 15 Aliyense amene adzapezedwe adzabooledwa ndipo aliyense amene adzagwidwe limodzi ndi anthu ena onse pa nthawiyo, adzaphedwa ndi lupanga.+ 16 Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa, iwo akuona.+ Katundu wa m’nyumba zawo adzalandidwa, ndipo akazi awo adzagwiriridwa.+
17 “Ndidzachititsa Amedi kuti awaukire.+ Iwowa amaona kuti siliva si kanthu, ndipo sasangalala ndi golide. 18 Ndi mauta awo, adzaphwanyaphwanya ngakhale anyamata awo.+ Iwo sadzamvera chisoni zipatso za m’mimba.+ Diso lawo silidzamvera chisoni ana aamuna. 19 Babulo, amene ndi chokongoletsera maufumu,+ chinthu chokongola ndi chonyadira cha Akasidi,+ adzakhala ngati pamene Mulungu anagonjetsa Sodomu ndi Gomora.+ 20 M’Babulo simudzakhalanso anthu,+ ndipo iye sadzakhalaponso ku mibadwomibadwo.+ Kumeneko Mluya sadzakhomako hema wake, ndipo abusa sadzagonekako ziweto zawo. 21 Nyama zam’tchire zokhala kumadera opanda madzi zidzagona kumeneko, ndipo nyumba za anthu amene anali kukhala kumeneko zidzadzaza ndi akadzidzi.+ Nthiwatiwa zizidzakhala kumeneko, ndipo ziwanda zooneka ngati mbuzi* zizidzadumphadumpha kumeneko.+ 22 Mimbulu izidzalira munsanja zake zokhalamo,+ ndipo njoka zikuluzikulu zizidzakhala m’nyumba zachifumu zokongola. Nyengo yake yatsala pang’ono kufika, ndipo masiku ake sadzatalikitsidwa.”+
14 Pakuti Yehova adzachitira chifundo Yakobo+ ndipo adzasankhanso Isiraeli.+ Iye adzawapatsa mpumulo m’dziko lawo.+ Alendo adzakhala nawo limodzi ndipo adzadziphatika kunyumba ya Yakobo.+ 2 Anthu a mitundu ina adzawatenga n’kubwerera nawo kwawo ndipo nyumba ya Isiraeli idzatenga anthuwo kuti akhale awo m’dziko la Yehova, ndiponso kuti akhale antchito awo aamuna ndi aakazi.+ Iwo adzagwira+ anthu amene anawagwira n’kupita nawo kudziko lina ndipo azidzalamulira anthu amene anali kuwagwiritsa ntchito.+
3 M’tsiku limene Yehova adzakupatseni mpumulo ku ululu wanu, ku nsautso yanu ndi ku ukapolo wowawa umene inu munalimo,+ 4 mudzanene mwambi uwu wotonza mfumu ya Babulo:
“Uja ankagwiritsa ntchito anzakeyu wasiya ndithu! Wopondereza uja waleka ndithu!+ 5 Yehova wathyola ndodo ya anthu oipa, ndodo ya anthu olamulira,+ 6 amene anali kumenya mwaukali anthu a mitundu yosiyanasiyana powakwapula mosalekeza,+ ndiponso amene anali kugonjetsa mitundu ya anthu mokwiya, ndi chizunzo chopanda malire.+ 7 Dziko lonse lapansi lapuma, lilibenso chosokoneza.+ Anthu akusangalala ndipo akufuula mokondwera.+ 8 Ngakhale mitengo ya mlombwa+ yakondwa poona zimene zakuchitikira. Nayonso mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni yakondwa, ndipo yonseyi yanena kuti, ‘Kuyambira pamene unagona pansi, palibenso munthu wodula mitengo+ amene wabwera kudzatidula.’
9 “Ngakhale Manda+ amene ali pansi agwedezeka kuti akumane nawe ukamabwera. Chifukwa cha iwe, mandawo adzutsa akufa,+ adzutsa olamulira onse a padziko lapansi okhala ngati mbuzi.+ Achititsa mafumu onse a mitundu ya anthu kunyamuka pamipando yawo yachifumu.+ 10 Onsewo akulankhula nawe kuti, ‘Kodi iwenso wafooketsedwa ngati ife?+ Kodi zoonadi wafanana ndi ife?+ 11 Kunyada kwako kwatsikira ku Manda limodzi ndi phokoso la zoimbira zako za zingwe.+ Mphutsi zayalana pansi pako ngati bedi, ndipo nyongolotsi zasanduka chofunda chako.’+
12 “Wagwa kuchokera kumwamba,+ wonyezimirawe, iwe mwana wa m’bandakucha! Wadulidwa n’kugwera padziko lapansi,+ iwe amene unali kupundula mitundu.+ 13 Iweyo wanena mumtima mwako kuti, ‘Ndikwera kumwamba.+ Ndikweza mpando wanga wachifumu+ pamwamba pa nyenyezi+ za Mulungu. Ndikhala paphiri lokumanapo+ kumapeto kwenikweni kwa madera a kumpoto.+ 14 Ndikwera pamwamba pamalo okwezeka a m’mitambo.+ Ndidzipanga kukhala wofanana ndi Wam’mwambamwamba.’+
15 “Koma adzakutsitsira ku Manda,+ pansi penipeni pa dzenje.+ 16 Okuona adzakuyang’ana modabwa. Adzakuyang’anitsitsa n’kunena kuti, ‘Kodi uyu ndi munthu amene anali kugwedeza dziko lapansi uja, amene anali kunjenjemeretsa maufumu,+ 17 amene anachititsa nthaka kukhala ngati chipululu, amene anagonjetsa mizinda ya padziko lapansi,+ ndiponso amene sanali kutsegulira njira akaidi ake kuti azipita kwawo?’+ 18 Mafumu ena onse a mitundu ya anthu anagona pansi mu ulemerero, aliyense m’manda ake.+ 19 Koma iweyo watayidwa popanda kuikidwa m’manda,+ ngati mphukira yonyansa imene ili pakati pa anthu akufa ophedwa ndi lupanga, amene akutsikira kumiyala ya m’dzenje.+ Watayidwa ngati mtembo wopondedwapondedwa.+ 20 Sudzakhalira nawo limodzi m’manda, chifukwa unawononga dziko lako lomwe, ndipo unapha anthu ako omwe. Mayina a ana a anthu ochita zoipa sadzatchulidwanso mpaka kalekale.+
21 “Anthu inu, konzekerani kupha ana ake chifukwa cha zolakwa za makolo awo,+ kuti asalandenso dziko lapansi n’kulidzaza ndi mizinda.”+
22 “Ine ndidzawaukira,”+ watero Yehova wa makamu.
“M’Babulo ndidzachotsamo dzina,+ anthu otsala, ana, ndi mbadwa,”+ watero Yehova.
23 “Babulo ndidzamusandutsa malo okhala nungu* ndiponso malo a zithaphwi. Ndidzamusesa ndi tsache* la chiwonongeko,”+ watero Yehova wa makamu.
24 Yehova wa makamu walumbira+ kuti: “Ndithu zimene ndaganiza zidzachitika, ndipo zimene ndakonza sizidzalephereka.+ 25 Ndidzathyola Msuri amene ali m’dziko langa+ ndipo ndidzamupondaponda pamapiri anga.+ Goli lake lidzachoka pa iwo ndipo katundu wake adzachoka pamapewa awo.”+
26 Izi ndi zimene ndatsimikiza kuchitira dziko lonse lapansi, ndipo ili ndi dzanja limene latambasuka kuti likanthe mitundu yonse ya anthu. 27 Pakuti Yehova wa makamu wagamula,+ ndani angazilepheretse?+ Dzanja lake n’limene latambasuka, ndani angalibweze?+
28 M’chaka chimene Mfumu Ahazi inamwalira,+ uthenga wamphamvu uwu unaperekedwa: 29 “Usasangalale+ iwe Filisitiya,+ kapena aliyense wokhala mwa iwe chifukwa chakuti ndodo ya amene anali kukumenya yathyoka.+ Pakuti pamuzu wa njokayo+ padzaphuka njoka yapoizoni,+ ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yothamanga, yaululu wamoto.+ 30 Ana oyamba kubadwa a anthu onyozeka, ndithu adzadya chakudya. Anthu osauka adzagona pansi popanda chowaopseza.+ Ndidzapha muzu wako ndi njala, ndipo amene adzatsale mwa iwe adzaphedwa.+ 31 Fuula chipata iwe! Lira mokweza mzinda iwe! Nonsenu mudzataya mtima, inu anthu okhala m’Filisitiya! Pakuti utsi ukubwera kuchokera kumpoto, ndipo palibe msilikali amene akutsalira pa magulu ake ankhondo.”+
32 Kodi munthu adzawayankha chiyani amithenga+ a mitundu ya anthu? Adzawayankha kuti, Yehova waika maziko a Ziyoni,+ ndipo anthu ake osautsika adzathawira mmenemo.
15 Uwu ndi uthenga wokhudza Mowabu:+ Chifukwa chakuti wasakazidwa usiku, Ari+ wa ku Mowabu wakhala chete. Chifukwa chakuti wasakazidwa usiku, Kiri+ wa ku Mowabu wakhala chete. 2 Iye wapita kukachisi ndi ku Diboni.+ Wapita kumalo okwezeka kukalira. Mowabu akulira mofuula chifukwa cha Nebo+ ndi Medeba.+ Anthu onse a mmenemo ameta mipala.+ Ndevu za munthu aliyense zametedwa. 3 Anthu avala ziguduli+ m’misewu yake. Pamadenga*+ ake ndi m’mabwalo a mizinda yake, aliyense akufuula. Akulira n’kumapita kumunsi.+ 4 Hesiboni ndi Eleyale+ akulira mofuula. Mawu awo amveka mpaka ku Yahazi.+ N’chifukwa chake amuna onyamula zida a ku Mowabu akungofuula. Mitima yawo ikuchita mantha kwambiri.
5 Mtima wanga ukulirira Mowabu.+ Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Aliyense akumakwera mtunda wa Luhiti+ akulira. Panjira yopita ku Horonaimu,+ iwo akufuula kwambiri chifukwa cha tsokalo. 6 Madzi a ku Nimurimu+ aumiratu. Msipu wauma. Udzu watha. Palibenso chobiriwira.+ 7 N’chifukwa chake akumanyamula zinthu zotsala ndi katundu amene anasunga, n’kumapita nazo kuchigwa* cha mitengo ya msondodzi. 8 Mfuu yamveka m’dziko lonse la Mowabu.+ Kufuula kwake kwamveka mpaka ku Egilaimu. Kufuula kwake kwamveka mpaka ku Beere-elimu, 9 chifukwa m’madzi onse a ku Dimoni mwadzaza magazi. Dimoni ndidzam’bweretsera zinthu zinanso, monga mikango yoti idye anthu othawa ku Mowabu ndi anthu otsala panthaka yawo.+
16 Anthu inu, tumizani nkhosa yamphongo kwa wolamulira wa dziko.+ Muitumize kuchokera ku Sela kudutsa kuchipululu mpaka kukafika kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.+
2 Pamalo owolokera chigwa cha Arinoni,+ ana aakazi a Mowabu adzakhala ngati mbalame yomwe ikuthawa, itathamangitsidwa pachisa chake.+
3 “Anthu inu, perekani malangizo. Chitani zimene zagamulidwa.+
“Chititsani kuti masana, mthunzi wanu uphimbe malo aakulu ndiponso uchititse mdima ngati wa usiku.+ Bisani anthu obalalika.+ Musaulule aliyense amene akuthawa.+ 4 Anthu anga obalalika akhale ngati alendo mwa iwe Mowabu.+ Iwo abisale mwa iwe pothawa wolanda,+ pakuti wopondereza anthu wafika pamapeto ake. Kulanda kwatha. Opondaponda anzawo atha padziko lapansi.+
5 “Mpando wachifumu ndithu udzakhazikika ndi kukoma mtima kosatha.+ Mfumu idzakhala pampandowo n’kumalamulira mokhulupirika muhema wa Davide.+ Izidzaweruza n’kumafunafuna chilungamo, ndipo izidzachita mwachangu zinthu zoyenera.”+
6 Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, kuti ndi wonyada kwambiri.+ Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, ndi mkwiyo wake.+ Zolankhula zake zodzitukumula sizidzachitika.+ 7 Chotero Mowabu adzalira mofuula chifukwa cha tsoka lake. Aliyense wokhala m’Mowabu ndithu adzalira mofuula.+ Omenyedwawo adzalirira mphesa zouma zoumba pamodzi za ku Kiri-hareseti,+ 8 chifukwa minda ya m’mapiri ya ku Hesiboni+ yafota. Eni ake a mitundu ya anthu athyola nthambi za mitengo ya mpesa ya ku Sibima+ zodzaza ndi mphesa zakupsa. Nthambizo zinafika mpaka ku Yazeri.+ Zinafika mpaka kuchipululu. Mphukira zake zinasiyidwa kuti zizingodzikulira pazokha. Zinafika mpaka kunyanja.
9 N’chifukwa chake ndidzalirire mtengo wa mpesa wa ku Sibima ngati mmene ndinachitira polirira Yazeri.+ Ndidzakunyowetsa kwambiri ndi misozi yanga iwe Hesiboni+ ndi Eleyale,+ chifukwa chakuti kufuula kwakugwera m’chilimwe ndi pa nthawi ya zokolola zako.+ 10 Kukondwera ndi kusangalala zachotsedwa m’munda wako wa zipatso, ndipo m’minda ya mpesa mulibe mfuu yachisangalalo. Mulibe aliyense amene akufuula.+ Mopondera mphesa mulibe amene akuponda vinyo.+ Ndachititsa kuti kufuula kulekeke.+
11 N’chifukwa chake mkati mwanga mukunjenjemera ngati zingwe za zeze chifukwa cha Mowabu,+ ndipo m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha Kiri-hareseti.+
12 Kenako zinaoneka kuti Mowabu anatopa pamalo okwezeka,+ ndipo anapita kumalo opatulika kukapemphera+ koma sizinathandize.+
13 Awa ndi mawu okhudza Mowabu amene Yehova ananena kalekale. 14 Koma tsopano Yehova wanena kuti: “Pomatha ndendende zaka zitatu,*+ ulemerero+ wa Mowabu udzatha. Iye adzachititsidwa manyazi ndipo adzakumana ndi chipwirikiti chamtundu uliwonse. Otsala mwa iye adzakhala ochepa kwambiri ndiponso opanda mphamvu.”+
17 Uwu ndi uthenga wokhudza Damasiko:+ “Taonani! Damasiko wachotsedwa kuti asakhalenso mzinda, ndipo wakhala bwinja, wakhala mulu wa zinthu zogumukagumuka.+ 2 Mizinda ya Aroweri+ imene yasiyidwa m’mbuyo yangosanduka malo okhala ziweto, kumene ziwetozo zimagona pansi popanda woziopsa.+ 3 Mu Efuraimu mulibenso mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri,+ ndipo mu Damasiko mulibenso ufumu.+ Ulemerero wa anthu otsala mu Siriya udzatha ngati ulemerero wa ana a Isiraeli,” akutero Yehova wa makamu.+
4 “M’tsiku limenelo, ulemerero wa Yakobo udzachepa,+ ndipo thupi lake lonenepa lidzaonda.+ 5 Munthu wokolola akamadzadula tirigu m’munda ndipo dzanja lake likamadzakolola ngala za tirigu,+ adzakhala ngati munthu wokunkha ngala za tirigu m’chigwa cha Arefai.+ 6 M’dzikolo mudzangotsala zokunkha ngati mmene zimatsalira mumtengo wa maolivi akaugwedeza: pamwamba pa nthambi padzangokhala maolivi awiri kapena atatu akupsa. Panthambi zobala zipatso padzangokhala maolivi anayi kapena asanu okha,” akutero Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+
7 M’tsiku limenelo, munthu wochokera kufumbi adzayang’ana kumwamba, kwa amene anamupanga. Maso ake adzayang’anitsitsa Woyera wa Isiraeli.+ 8 Iye sadzayang’ana maguwa a nsembe,+ omwe ndi ntchito ya manja ake.+ Sadzayang’anitsitsa zimene zala zake zapanga, kaya mizati yopatulika kapena maguwa ofukizirapo zonunkhira.+ 9 M’tsiku limenelo mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzakhala ngati malo amene angosiyidwa m’nkhalango. Idzakhala ngati nthambi imene anthu angoisiya chifukwa cha ana a Isiraeli, ndipo idzakhala bwinja.+ 10 Popeza waiwala+ Mulungu wa chipulumutso chako,+ ndipo Thanthwe+ la chitetezo chako sunalikumbukire, n’chifukwa chake ukulima minda yokongola n’kumabzalamo mphukira ya mlendo. 11 Masana ukhoza kuumangira mpanda wabwino munda wakowo, ndipo m’mawa ukhoza kuchititsa mbewu yako kuti iphuke. Koma zokolola zake zidzathawa m’tsiku la matenda ndi ululu wosachiritsika.+
12 Tsoka kwa mitundu ya anthu ambirimbiri amene akuchita chipwirikiti, amene akuwinduka ngati nyanja. Tsoka kwa magulu a mitundu ya anthu aphokoso, amene akusokosera ngati mkokomo wa madzi amphamvu.+ 13 Mitundu ya anthu+ idzasokosera ngati mkokomo wa madzi ambiri. Iye adzawadzudzula,+ ndipo iwo adzathawira kutali. Adzathamangitsidwa ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo m’mapiri ndiponso adzauluzika ngati tizitsotso touluzika ndi mphepo yamkuntho.+ 14 Madzulo kudzakhala zoopsa zamwadzidzidzi. Kusanache, zidzachoka.+ Izi n’zimene zidzachitikire anthu otilanda zinthu, ndipo n’zimene zidzagwere anthu oba katundu wathu.+
18 Tsoka kwa dziko lamkokomo wa tizilombo tamapiko, limene lili m’chigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya.+ 2 Limeneli ndi dziko lomwe limatumiza nthumwi zake+ panyanja, m’ngalawa zoyenda pamadzi zopangidwa ndi gumbwa.* Limauza nthumwizo kuti: “Inu amithenga achangu, pitani ku mtundu wa anthu ataliatali osalala, anthu oopedwa ndi mitundu yonse ya anthu. Umenewu ndi mtundu wa anthu amphamvu kwambiri, ndiponso wopambana pa nkhondo, umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje.”+
3 Inu nonse okhala panthaka ndi inu okhala m’dziko lapansi,+ mudzaona chinthu chooneka ngati chizindikiro chimene chimaikidwa pamapiri,+ ndipo mudzamva zofanana ndi kulira kwa lipenga.+ 4 Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Ine ndidzakhala mosatekeseka n’kumayang’ana pamalo anga okhazikika.+ Ndidzachita zimenezi ngati kutentha kumene kumakhalapo masana kukawala,+ ndiponso ngati mame amene amagwa pa nthawi yokolola, m’nyengo yotentha.+ 5 Pakuti nyengo yokolola isanafike, mitengo ikamaliza kuchita maluwa ndipo mphesa zikamapsa, mlimi amadula mphukira ndi chida chosadzira mitengo ndipo amasadzanso nthambi.+ 6 Onsewo adzasiyidwa kuti mbalame za m’mapiri zodya nyama, ndi nyama zakutchire za padziko lapansi,+ ziwadye. Mbalame zodya nyamazo zidzakhala zikuwadya chilimwe chonse, ndipo nyama zonse zakutchire za padziko lapansi zidzakhala zikuwadya m’nyengo yonse yokolola.+
7 “Pa nthawi imeneyo, Yehova wa makamu+ adzapatsidwa mphatso ndi mtundu wa anthu ataliatali osalala, anthu oopedwa+ ndi mitundu yonse ya anthu. Umenewu ndi mtundu wa anthu amphamvu kwambiri, ndiponso wopambana pa nkhondo, umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje. Mphatsoyo adzaiika kuphiri la Ziyoni, kumene kuli dzina la Yehova wa makamu.”+
19 Uwu ndi uthenga wokhudza Iguputo:+ Taonani! Yehova wakwera mtambo wothamanga+ ndipo akubwera mu Iguputo. Milungu yopanda pake ya ku Iguputo idzanjenjemera chifukwa chomuopa+ ndipo mitima ya Aiguputo idzasungunuka mkati mwa dzikolo.+
2 “Ndidzachititsa kuti Aiguputo ayambane ndi Aiguputo anzawo. Aliyense adzamenyana ndi m’bale wake ndipo aliyense adzamenyana ndi mnzake. Mzinda udzamenyana ndi mzinda unzake ndipo ufumu udzamenyana ndi ufumu unzake.+ 3 Anthu a mu Iguputo adzadabwa kwambiri+ ndipo ine ndidzasokoneza zolinga za dzikolo.+ Iwo adzafunsira kwa milungu yopanda pake,+ kwa anthu amatsenga, kwa olankhula ndi mizimu ndiponso kwa olosera zam’tsogolo.+ 4 Ndidzapereka Iguputo m’manja mwa mbuye wankhanza ndipo mfumu imene idzawalamulire idzakhala yamphamvu,”+ akutero Ambuye woona, Yehova wa makamu.
5 Madzi adzauma m’nyanja, ndipo mtsinje udzakhala wopanda madzi ndi wouma.+ 6 Mitsinje idzanunkha. Ngalande za ku Iguputo zochokera mumtsinje wa Nailo zidzaphwa ndipo zidzauma.+ Bango+ ndi udzu* zidzafota. 7 Madambo a m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo, malo othera mtsinje wa Nailo, ndi malo onse obzala mbewu m’mphepete mwa mtsinjewo, adzauma.+ Zomera za m’mphepete mwa mtsinjewo zidzauma ndipo zidzauluzika ndi mphepo. 8 Asodzi a nsomba adzalira ndipo onse oponya mbedza mumtsinje wa Nailo adzamva chisoni. Ngakhale oponya maukonde ophera nsomba pamadziwo adzalefuka.+ 9 Anthu amene amagwiritsira ntchito fulakesi*+ wopalapala pa ntchito yawo adzachita manyazi. Anthu owomba nsalu yoyera adzachitanso manyazi. 10 Anthu ake owomba nsalu+ adzavutika maganizo. Anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzamva chisoni mumtima.
11 Akalonga a ku Zowani+ ndi opusa ndithu. Malangizo a anthu anzeru ochokera pakati pa alangizi a Farao, ndi osathandiza.+ Kodi anthu inu mudzamuuza bwanji Farao kuti: “Ine ndine mwana wa anthu anzeru, mwana wa mafumu akale”? 12 Kodi anthu ako anzeruwo ali kuti?+ Ngati akudziwa, akuuze zimene Yehova wa makamu wakonza zokhudza Iguputo.+ 13 Akalonga a ku Zowani achita zopusa.+ Akalonga a ku Nofi+ anyengezedwa. Atsogoleri+ a mafuko achititsa Iguputo kuyenda uku ndi uku. 14 Yehova waika mzimu wachisokonezo pakati pa dzikolo.+ Atsogoleri awo achititsa Iguputo kuyenda uku ndi uku m’zochita zake zonse, ngati munthu woledzera amene akuterereka m’masanzi ake.+ 15 Sipadzakhala chilichonse choti Iguputo achite, choti mutu kapena mchira komanso mphukira ndi udzu zichite.+
16 M’tsiku limenelo, Aiguputo adzakhala ngati akazi. Iwo adzanjenjemera+ ndi kuchita mantha, chifukwa Yehova wa makamu adzawatambasulira dzanja lake.+ 17 Dziko la Yuda lidzakhala chinthu choopseza Iguputo.+ Aliyense amene wauzidwa za dzikolo, akuchita mantha chifukwa cha zimene Yehova wa makamu watsimikiza kuwachitira.+
18 M’tsiku limenelo, padzakhala mizinda isanu m’dziko la Iguputo+ yolankhula chinenero cha ku Kanani+ ndiponso yolumbira+ kwa Yehova wa makamu. Mzinda umodzi udzatchedwa Mzinda wa Chiwonongeko.
19 M’tsiku limenelo, m’dziko la Iguputo mudzakhala guwa lansembe la Yehova,+ ndipo m’malire mwake mudzakhala chipilala cha Yehova. 20 Zimenezi zidzakhala chizindikiro ndi umboni kwa Yehova wa makamu m’dziko la Iguputo,+ pakuti iwo adzalirira Yehova chifukwa cha anthu owapondereza,+ ndipo iye adzawatumizira mpulumutsi wamkulu amene adzawapulumutse.+ 21 Yehova adzadziwika bwino kwa Aiguputo,+ ndipo Aiguputowo adzamudziwa Yehova m’tsiku limenelo. Iwo adzapereka nsembe ndi mphatso+ ndiponso adzachita lonjezo kwa Yehova n’kulikwaniritsa.+ 22 Yehova adzakantha Iguputo.+ Adzamukantha n’kumuchiza,+ ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova.+ Iye adzamva kuchonderera kwawo ndipo adzawachiritsa.+
23 M’tsiku limenelo, padzakhala msewu waukulu+ wochokera ku Iguputo kupita ku Asuri. Anthu a ku Asuri adzapita ku Iguputo ndipo anthu a ku Iguputo adzapita ku Asuri. Aiguputo ndi Asuri adzatumikira Mulungu limodzi. 24 M’tsiku limenelo, Isiraeli adzakhala gawo limodzi mwa magawo atatu, pamodzi ndi Iguputo ndi Asuri,+ kutanthauza kuti adzakhala dalitso padziko lapansi,+ 25 popeza Yehova wa makamu adzawadalitsa+ n’kuwauza kuti: “Adalitsike Aiguputo anthu anga, Asuri+ ntchito ya manja anga, ndi Aisiraeli cholowa changa.”+
20 M’chaka chimene Tatani*+ anapita ku Asidodi,+ atatumidwa ndi Sarigoni mfumu ya Asuri,+ n’kukamenyana ndi mzinda wa Asidodi n’kuulanda,+ 2 pa nthawi imeneyo Yehova analankhula kudzera mwa Yesaya mwana wa Amozi,+ kuti: “Pita+ ukavule chiguduli chimene chili m’chiuno mwako+ ndipo ukavulenso nsapato zimene zili kuphazi kwako.”+ Iye anakachitadi zimenezo, n’kumayenda wopanda zovala* ndiponso wopanda nsapato.+
3 Kenako Yehova anati: “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wayendera wopanda zovala ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu, kuti akhale chizindikiro+ ndi chenjezo kwa Iguputo+ ndi Itiyopiya,+ 4 momwemonso mfumu ya Asuri idzagwira gulu la anthu ku Iguputo+ ndi ku Itiyopiya n’kupita nawo ku ukapolo kudziko lina, anyamata ndi nkhalamba, ali opanda zovala ndi opanda nsapato, ndiponso matako awo ali pamtunda. Pamenepo, umaliseche wa Iguputo udzaonekera.+ 5 Iwo adzachita mantha ndiponso manyazi chifukwa chakuti anali kudalira Itiyopiya+ komanso chifukwa chakuti anali kusirira kukongola kwa Iguputo.+ 6 M’tsiku limenelo, munthu wokhala m’dziko lino la m’mphepete mwa nyanja adzati, ‘Taonani zimene zachitikira dziko limene tinali kulidalira lija, limene tinathawirako kuti litithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya Asuri.+ Ndiye ifeyo atipulumutse ndani?’”
21 Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu cha nyanja:*+ Kuchipululu kukubwera chinthu chinachake kuchokera kudziko lochititsa mantha.+ Chikubwera ngati mphepo yamkuntho+ yochokera kum’mwera. 2 Pali masomphenya ochititsa mantha+ amene ndaona: Mtundu wochita chinyengo ukuchita zachinyengo, ndipo mtundu wolanda zinthu ukulanda zinthu.+ Pita ukachite nkhondo, iwe Elamu! Kazungulire mzindawo, iwe Mediya!+ Ndathetsa kuusa moyo* konse kumene mzindawo unachititsa.+ 3 N’chifukwa chake m’chiuno mwanga mwadzaza ululu woopsa.+ Zopweteka zandigwira, ngati zowawa za mkazi amene akubereka.+ Ndazunguzika moti sindikumva. Ndasokonezeka moti sindikuona. 4 Mtima wanga ukuthamanga. Ndikunjenjemera ndi mantha. Chisisira cha madzulo chimene ndinali kuchikonda chakhala chondichititsa mantha.+
5 Yalani patebulo. Ikani mipando m’malo mwake. Idyani, imwani.+ Akalonga inu,+ nyamukani, dzozani chishango.+ 6 Pakuti Yehova wandiuza kuti:
“Pita, kaike mlonda pamalo ake, kuti anene zonse zimene aone.”+
7 Mlondayo anaona magaleta ankhondo okokedwa ndi mahatchi awiriawiri, magaleta ankhondo okokedwa ndi abulu, ndi magaleta ankhondo okokedwa ndi ngamila. Iye anali kuyang’anitsitsa, ndipo anali tcheru kwambiri. 8 Kenako anafuula mwamphamvu ngati kubangula kwa mkango,+ kuti: “Inu Yehova, ine ndimaimirira tsiku lonse pansanja ya mlonda, ndipo usiku uliwonse ndimakhala pamalo anga olonderapo.+ 9 Tsopano taonani! Kukubwera magaleta ankhondo okokedwa ndi mahatchi awiriawiri, mutakwera amuna ankhondo.”+
Kenako iye anayamba kufuula kuti: “Wagwa! Babulo wagwa!+ Zifaniziro zonse zogoba za milungu yake zaphwanyidwa ndipo zili pansi.”+
10 Inu anthu anga amene mwapunthidwa ngati mbewu, ndi iwe mwana wa pamalo anga opunthira mbewu,+ zimene ndamva kwa Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, n’zimene ndakuuzani anthu inu.
11 Uwu ndi uthenga wokhudza Duma: Ndikumva winawake akundifunsa mofuula kuchokera ku Seiri+ kuti: “Mlonda, kodi usiku watsala wotalika bwanji? Mlonda, kodi usiku watsala wotalika bwanji?”+ 12 Mlondayo anayankha kuti: “M’mawa ufika, ndipo usiku ufikanso. Ngati anthu inu mukufuna kufunsa, funsani ndipo mubwerenso.”
13 Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu: Inu amuna amtengatenga a ku Dedani oyenda pa ngamila, usiku mudzagona m’nkhalango ya m’chipululu.+ 14 Mubweretse madzi podzakumana ndi munthu waludzu. Inu anthu okhala ku Tema,+ mukhale ndi chakudya podzakumana ndi munthu amene akuthawa. 15 Pakuti iwo athawa chifukwa cha malupanga, chifukwa cha lupanga losololedwa m’chimake, chifukwa cha uta wopindidwa, ndiponso chifukwa cha kukula kwa nkhondo.
16 Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Pakutha chaka chimodzi, osawonjezerapo ngakhale tsiku limodzi,*+ ulemerero wonse wa Kedara+ udzakhala utatha. 17 Anthu otsala pa amuna oponya mivi ndi uta, omwe ndi amuna amphamvu a ana a Kedara, adzakhala ochepa,+ pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena zimenezi.”+
22 Uwu ndi uthenga wokhudza chigwa cha masomphenya:+ Kodi chachitika n’chiyani kuti anthu ako onse akwere pamadenga?+ 2 Iwe unali mzinda wodzaza ndi chipwirikiti, waphokoso, komanso unali mudzi wokondwa.+ Anthu ako amene aphedwa, sanaphedwe ndi lupanga ndiponso sanaphedwe kunkhondo.+ 3 Olamulira ako onse ankhanza+ athawa nthawi imodzi.+ Atengedwa ukaidi popanda kugwiritsa ntchito uta. Anthu ako onse amene apezeka atengedwa ukaidi limodzi.+ Iwo anali atathawira kutali.
4 N’chifukwa chake ndanena kuti: “Musandiyang’anitsitse. Ine ndikulira mopwetekedwa mtima+ ndipo anthu inu musaumirire kunditonthoza pamene ndikulirira mwana wamkazi wa anthu anga, yemwe walandidwa katundu.+ 5 Pakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, wabweretsa tsiku lachisokonezo,+ la kugonjetsedwa+ ndiponso lothetsa nzeru+ m’chigwa cha masomphenya. Kumeneko mpanda ukugwetsedwa+ ndipo kufuula kukumvekera m’phiri.+ 6 Elamu+ watenga kachikwama koikamo mivi. Iye wakwera galeta lankhondo lonyamula anthu lokokedwa ndi mahatchi, ndipo Kiri+ wasolola chishango. 7 M’zigwa zako zabwino koposa mudzadzaza magaleta ankhondo. Ndithu mahatchi adzaima m’malo awo pachipata, 8 ndipo wina adzachotsa chophimba cha Yuda. M’tsiku limenelo, udzayang’ana kunyumba ya nkhalango yosungiramo zida zankhondo.+ 9 Anthu inu mudzaona ming’alu ya Mzinda wa Davide pakuti idzakhala yambiri,+ ndipo mudzatunga madzi a m’dziwe lakumunsi.+ 10 Mudzawerenga nyumba za ku Yerusalemu ndipo mudzagwetsanso nyumba kuti mulimbitsire khoma lake.+ 11 Mudzakumba dziwe pakati pa makoma awiri, losungiramo madzi a dziwe lakale.+ Simudzayang’ana Wolipanga Wamkulu ndipo amene analipanga kalekalelo simudzamuona.
12 “M’tsiku limenelo, Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ adzalamula anthu kuti alire,+ agwetse misozi, amete mipala ndiponso avale ziguduli m’chiuno.+ 13 Komatu anthuwo adzakondwera ndi kusangalala. Adzapha ng’ombe ndi nkhosa. Adzadya nyama ndi kumwa vinyo.+ Iwo adzati, ‘Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.’”+
14 Yehova wa makamu wandiuza+ kuti: “‘Cholakwa ichi sichidzaphimbidwa+ kufikira anthu inu mutafa.’+ Akutero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.”
15 Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pita kwa Sebina,+ kapitawo woyang’anira nyumba ya mfumu,+ ukamuuze kuti, 16 ‘Kodi kuno kuli wachibale wako aliyense, ndipo kodi m’bale wako anaikidwa kuno kuti iweyo udzigobere manda kunoko?’+ Iye wagoba manda ake pamwamba pa phiri lamiyala. Akudzikonzera malo opumulirako m’thanthwe. 17 ‘Iwe mwamuna wamphamvu, tamvera! Yehova akuponya pansi mwamphamvu, ndipo akugwira mwamphamvu. 18 Ndithu iye adzakukulunga mwamphamvu ngati mpira n’kukuponyera kudziko lalikulu. Iweyo udzafera kumeneko ndipo magaleta ako ankhondo aulemerero adzakhala ochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako. 19 Ndidzakuchotsa pampando wako ndipo munthu wina adzakukokera pansi n’kukuchotsa pa udindo wako.+
20 “‘M’tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga+ Eliyakimu,+ mwana wa Hilikiya.+ 21 Iyeyo ndidzamuveka mkanjo wako ndipo lamba wako ndidzamumanga mwamphamvu m’chiuno mwake.+ Ulamuliro wako ndidzaupereka m’manja mwake ndipo iye adzakhala tate wa anthu okhala mu Yerusalemu ndi a m’nyumba ya Yuda.+ 22 Ndidzaika makiyi+ a nyumba ya Davide paphewa pake. Iye akatsegula palibe amene azidzatseka ndipo akatseka palibe amene azidzatsegula.+ 23 Ndidzamukhomerera ngati chikhomo pamalo okhalitsa.+ Iye adzakhala ngati mpando wachifumu waulemerero kunyumba ya bambo ake.+ 24 Anthu adzapachika pa iyeyo ulemerero wonse wa nyumba ya bambo ake: mbadwa ndi mphukira, kutanthauza mitundu yonse ya ziwiya zing’onozing’ono, mitundu yonse ya ziwiya zolowa, ndi mitundu yonse ya mitsuko ikuluikulu.’
25 “Yehova wa makamu wanena kuti: ‘M’tsiku limenelo chikhomo+ chimene chinakhomedwa pamalo okhalitsa chidzachotsedwa.+ Chidzazulidwa ndipo chidzagwa pansi. Katundu amene anapachikidwapo adzagwa pansi n’kuwonongeka, pakuti Yehova ndiye wanena zimenezi.’”+
23 Uthenga wokhudza Turo:+ Lirani mofuula inu zombo za ku Tarisi,+ chifukwa chakuti mzindawo wasakazidwa ndipo sulinso doko. Sulinso malo oti mungafikepo.+ Anthu amva zimenezi ali kudziko la Kitimu.+ 2 Khalani chete inu anthu okhala m’mphepete mwa nyanja. Amalonda a ku Sidoni,+ amene amawoloka nyanja, akulemeretsani. 3 Mbewu za ku Sihori+ ndi zokolola za kumtsinje wa Nailo, zimene zinali kuyenda pamadzi ambiri ndiponso zimene zinali kukubweretserani ndalama, zakhala phindu la mitundu ina ya anthu.+
4 Chita manyazi iwe Sidoni,+ ndiponso iwe malo achitetezo a m’mbali mwa nyanja, chifukwa nyanja yanena kuti: “Sindinamvepo zowawa za pobereka, ndipo sindinaberekepo. Sindinalerepo anyamata kapena anamwali.”+ 5 Anthu adzamva chisoni chachikulu akadzamva za Turo,+ ngati mmene anamvera chisoni atamva za Iguputo.+ 6 Wolokerani ku Tarisi. Lirani mofuula, inu anthu okhala m’mphepete mwa nyanja. 7 Kodi uwu ndi mzinda wanu uja, umene unali wosangalala kuyambira kalekale, kuyambira pa chiyambi pake? Mapazi ake anali kuutengera kutali kuti ukakhale ngati mlendo.
8 Ndani wapereka chigamulo+ chotsutsana ndi Turo, mzinda umene unali kuveka anthu zisoti zachifumu, umene amalonda ake anali akalonga, ndiponso umene ochita malonda ake anali anthu olemekezeka a padziko lapansi?+
9 Yehova wa makamu ndi amene wapereka chigamulo chimenechi,+ kuti anyansitse kukongola kwa mzindawo ndi kuchotsa kunyada kwake,+ ndiponso kuti anyoze anthu onse olemekezeka a padziko lapansi.+
10 Iwe mwana wamkazi wa Tarisi,+ sefukira m’dziko lako ngati kusefukira kwa mtsinje wa Nailo. Kulibenso doko la zombo zapanyanja.+ 11 Mulungu watambasulira dzanja lake panyanja. Wagwedeza maufumu.+ Yehova walamula kuti malo achitetezo a ku Foinike awonongedwe.+ 12 Iye wati: “Usadzakondwerenso+ namwaliwe, mwana wamkazi wa Sidoni+ woponderezedwa. Nyamuka, wolokera ku Kitimu.+ Koma ngakhale kumeneko, sukapezako mpumulo.”
13 Taonani dziko la Akasidi.+ Anthu awa, osati Asuri,+ ndi amene anapanga mzindawo kuti ukhale malo okhala nyama zam’chipululu.+ Amanga nsanja zawo zomenyerapo nkhondo.+ Agumula nyumba zake zachifumu.+ Iwo asandutsa mzindawo bwinja logumukagumuka.+
14 Inu zombo za ku Tarisi, lirani mofuula chifukwa malo anu achitetezo asakazidwa.+
15 M’tsiku limenelo, Turo adzaiwalidwa kwa zaka 70.+ Zimenezi ndi zaka za ulamuliro wa mfumu imodzi. Pamapeto pa zaka 70 zimenezo, Turo adzakhala ngati hule wa m’nyimbo yakuti: 16 “Iwe hule amene unaiwalidwa, tenga zeze n’kumazungulira mumzinda.+ Yesetsa kuimba zezeyo mwaluso. Imba nyimbo zambiri kuti ukumbukiridwe.”
17 Pamapeto pa zaka 70, Yehova adzakumbukira Turo. Mzindawo udzayambiranso kulandira malipiro+ ndipo udzachita uhule ndi maufumu onse a padziko lapansi.+ 18 Phindu lake ndi malipiro ake+ zidzakhala zopatulika kwa Yehova. Phindu lakelo silidzasungidwa kapena kukundikidwa chifukwa malipiro ake adzakhala a anthu okhala pamaso pa Yehova,+ kuti anthuwo azidya mpaka kukhuta ndiponso kuti azivala zovala zokongola.+
24 Taonani! Yehova akuchotsa anthu onse m’dziko n’kulisiya lopanda kanthu.+ Iye wawononga dzikolo,+ n’kubalalitsa anthu okhalamo.+ 2 Zidzakhala chimodzimodzi kwa anthuwo ndi kwa wansembe, kwa wantchito ndi kwa mbuye wake, kwa wantchito wamkazi ndi kwa mbuye wake wamkazi, kwa wogula ndi kwa wogulitsa, kwa wobwereketsa ndi kwa wobwereka, kwa wolandira chiwongoladzanja ndi kwa wopereka chiwongoladzanja.+ 3 Anthu onse adzachotsedwa ndithu m’dzikolo ndipo katundu yense wa m’dzikolo adzatengedwa,+ pakuti Yehova ndiye wanena mawu amenewa.+ 4 Dzikolo likulira+ ndipo likuzimiririka. Nthaka ya dziko lapansi yafota ndipo yazimiririka. Anthu apamwamba a m’dzikolo afota.+ 5 Dzikolo laipitsidwa ndi anthu okhalamo,+ chifukwa alambalala malamulo,+ asintha malamulowo+ ndipo aphwanya pangano limene linayenera kukhalapo mpaka kalekale.+ 6 N’chifukwa chake temberero lameza dzikolo,+ ndipo anthu okhala m’dzikolo apezeka ndi mlandu. Chotero anthu okhala m’dzikolo achepamo, ndipo anthu amene atsalamo ndi ochepa kwambiri.+
7 Vinyo watsopano akulira, ndipo mtengo wa mpesa wafota.+ Anthu onse amene anali kusangalala mumtima mwawo akuusa moyo.+ 8 Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi maseche zasiya kumveka. Phokoso la anthu okondwa kwambiri silikumvekanso. Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi zeze zaleka kumveka.+ 9 Anthu akumwa vinyo popanda nyimbo. Akamamwa chakumwa choledzeretsa, akumachimva kuwawa. 10 Mudzi umene anthu ake anachokamo wawonongedwa.+ Nyumba iliyonse yatsekedwa kuti munthu asalowemo. 11 Anthu akulira m’misewu chifukwa chosowa vinyo. Kusangalala konse kwatha. Chisangalalo cha dzikolo chachoka.+ 12 Panopa mumzindawo mukudabwitsa kwambiri. Chipata chaphwanyidwa ndipo changokhala mulu wazinyalala.+
13 Chotero pakatikati pa dzikolo, pakati pa anthu a mitundu ina, anthu anga adzakhala ngati zipatso zotsala mumtengo wa maolivi,+ ndiponso ngati zokunkha zotsala anthu akakolola mphesa.+ 14 Iwo adzafuula mosangalala. Adzafuula mokondwa ali kunyanja, chifukwa cha kukwezeka kwa Yehova.+ 15 N’chifukwa chake iwo adzalemekeze Yehova+ m’chigawo cha kuwala.*+ M’zilumba zakunyanja adzalemekeza dzina la Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli. 16 Tamva nyimbo zikuimbidwa kumalekezero a dziko kuti:+ “Chokongoletsera ulemerero wa Wolungama.”+
Koma ine ndinati: “Ndatheratu!+ Ndatheratu ine! Kalanga ine! Anthu ochita zachinyengo achita zachinyengo.+ Iwo achita mwachinyengo pochita zinthu zachinyengo.”+
17 Mantha, dzenje ndi msampha zili pa iwe, munthu wokhala m’dzikoli.+ 18 Aliyense wothawa phokoso la chinthu chochititsa mantha adzagwera m’dzenje,+ ndipo aliyense wotuluka m’dzenjemo adzagwidwa mumsampha. Pakuti zotsekera madzi akumwamba zidzatseguka+ ndipo maziko a dziko adzagwedezeka.+ 19 Dzikolo lang’alukiratu, lagwedezekeratu, lili dzandidzandi.+ 20 Dzikolo likudzandira ngati munthu woledzera. Likugwedezekera uku ndi uku ngati chisimba.+ Zolakwa za dzikolo n’zolemera+ ndipo lidzagwa nazo osadzukanso.+
21 M’tsiku limenelo Yehova adzakumbukira makamu akumwamba ndi mafumu a padziko lapansi.+ 22 Iwo adzasonkhanitsidwa ngati akaidi amene akuwasonkhanitsira m’dzenje.+ Adzatsekeredwa m’ndende,+ ndipo pakadzapita masiku ochuluka adzakumbukiridwanso.+ 23 Mwezi wathunthu wachita manyazi. Dzuwa lowala lachitanso manyazi,+ pakuti Yehova wa makamu wakhala mfumu+ yaulemerero m’phiri la Ziyoni+ ndi mu Yerusalemu, pamaso pa anthu ake achikulire.+
25 Inu Yehova, ndinu Mulungu wanga.+ Ndikukukwezani+ ndi kutamanda dzina lanu+ chifukwa mwachita zinthu zabwino kwambiri.+ Mwakwaniritsa zolinga zanu+ zakalekale ndipo mwachita zinthu mokhulupirika+ ndi modalirika.+ 2 Mwasandutsa mzinda kukhala mulu wamiyala ndipo mudzi wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mwausandutsa bwinja logumukagumuka. Mzinda wa chitetezo champhamvu wa anthu achilendo mwauthetsa ndipo sudzamangidwanso mpaka kalekale.+ 3 N’chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani. Mudzi wa mitundu yankhanza udzakuopani.+ 4 Pakuti inu mwakhala malo achitetezo kwa munthu wonyozeka ndiponso malo achitetezo kwa munthu wosauka m’masautso ake.+ Mwakhala malo ousapo mvula yamkuntho ndi mthunzi+ wobisalirapo kutentha kwa dzuwa. Mwakhala wotero pamene anthu ankhanza akuwomba anzawo ngati mvula yamkuntho yowomba khoma. 5 Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsera kutentha m’dziko lopanda madzi, inu mumachepetsa phokoso la alendo.+ Nayonso nyimbo ya anthu ankhanza yaletsedwa.+
6 Yehova wa makamu adzakonzera anthu a mitundu yonse+ m’phiri ili,+ phwando la zakudya zabwinozabwino,+ phwando la vinyo wokoma kwambiri,* phwando la zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta a m’mafupa,+ ndiponso la vinyo+ wokoma kwambiri, wosefedwa bwino.+ 7 M’phiri limeneli iye adzameza chophimba chimene chikuphimba anthu onse,+ ndi nsalu imene yakuta mitundu yonse. 8 Iye adzameza imfa kwamuyaya+ ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.+ Adzachotsa kunyozeka kwa anthu ake padziko lonse lapansi,+ pakuti Yehova ndiye wanena zimenezi.
9 M’tsiku limenelo munthu adzati: “Taonani! Uyu ndiye Mulungu wathu.+ Chiyembekezo chathu chinali mwa iye+ ndipo iye watipulumutsa.+ Uyu ndi Yehova.+ Chiyembekezo chathu chinali mwa iye. Tiyeni tisangalale ndi kukondwera ndi chipulumutso chochokera kwa iye.”+
10 Pakuti dzanja la Yehova lidzakhazikika paphiri limeneli,+ ndipo Mowabu adzapondedwapondedwa+ pamalo pake ngati mulu wa udzu umene umapondedwapondedwa pamalo opangira manyowa.+ 11 Iye adzatambasula manja ake n’kuwamenyetsa pakati pa mzindawo ngati mmene munthu wosambira amatambasulira manja ake n’kuwamenyetsa pamadzi akamasambira. Adzathetsa kunyada+ kwa mzindawo poumenya mwaluso ndi manja ake. 12 Iye adzagwetsa mzinda wokhala ndi mipanda yachitetezo italiitali yolimba kwambiri. Adzautsitsa n’kuugwetsera pansi, pafumbi.+
26 M’tsiku limenelo,+ m’dziko la Yuda+ mudzaimbidwa nyimbo+ yakuti: “Ife tili ndi mzinda wolimba.+ Iye waika chipulumutso ngati mipanda ndiponso ngati chiunda chomenyerapo nkhondo.*+ 2 Anthu inu, tsegulani zipata+ kuti mtundu wolungama, umene ukuchita zinthu mokhulupirika ulowe.+ 3 Anthu amene ali ndi mtima wosagwedezeka mudzawateteza powapatsa mtendere wosatha,+ chifukwa amadalira inu.+ 4 Anthu inu muzidalira Yehova+ nthawi zonse, pakuti Ya* Yehova ndiye Thanthwe+ mpaka kalekale.
5 “Pakuti iye watsitsa anthu okhala pamalo okwezeka,+ okhala m’mudzi wokwezeka.+ Mudziwo wautsitsa. Wautsitsira pansi, waugwetsa mpaka pafumbi.+ 6 Phazi lidzaupondaponda. Mapazi a munthu wosautsika ndi mapazi a anthu onyozeka, adzaupondaponda.”+
7 Njira ya munthu wolungama ndi yowongoka.+ Popeza inu ndinu wochita zowongoka, mudzasalaza njira ya munthu wolungama.+ 8 Inu Yehova, ife tayembekezera inu pofunafuna njira yanu ya chilungamo.+ Mtima wathu wakhala ukulakalaka kuti ukumbukire dzina lanu, ndi zimene dzinalo limaimira.+ 9 Usiku, mtima wanga umakulakalakani.+ Ndithu ndimakufunafunani ndi mtima wonse,+ chifukwa mukadzaweruza dziko lapansi,+ anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzira chilungamo.+ 10 Ngakhale munthu woipa atachitiridwa zabwino, sangaphunzire chilungamo.+ M’dziko lochita zowongoka, iye adzachita zinthu zopanda chilungamo+ ndipo sadzaona ukulu wa Yehova.+
11 Inu Yehova, dzanja lanu lakwezeka,+ koma iwo sakuliona.+ Iwo adzaona mmene mukudziperekera kwa anthu anu, ndipo adzachita manyazi.+ Ndithu, moto+ wanu udzanyeketsa adani anu. 12 Inu Yehova, mudzachita chilungamo kuti mutipatse mtendere,+ pakuti ntchito zathu zonse tazikwanitsa chifukwa cha inu.+ 13 Inu Yehova Mulungu wathu, ife takhalapo m’manja mwa ambuye ena kupatula inu.+ Koma chifukwa cha thandizo lanu, timatha kutchula dzina lanu.+ 14 Iwo afa. Sadzakhalanso ndi moyo.+ Iwo ndi akufa+ ndipo sadzaukanso.+ Pa chifukwa chimenechi, mwawatembenukira kuti muwawononge n’cholinga choti asadzatchulidwenso.+
15 Mwakulitsa mtundu, inu Yehova. Mwakulitsa mtundu+ ndipo mwadzilemekeza.+ Mwafutukulira kutali malire onse a dzikolo.+ 16 Inu Yehova, pa nthawi ya masautso iwo atembenukira kwa inu.+ Mutawalanga, akhuthulira mitima yawo kwa inu m’pemphero lonong’ona.+ 17 Chifukwa cha inu Yehova, ife takhala ngati mkazi wapakati amene watsala pang’ono kubereka, amene akumva zowawa za pobereka, amene akulira ndi ululu wa pobereka.+ 18 Ife tinali ndi pakati, tinamva zowawa za pobereka,+ koma takhala ngati tabereka mphepo. Palibe chipulumutso chenicheni chimene tapeza m’dzikoli,+ ndipo sitikuberekanso anthu ena oti akhale panthaka ya dziko lapansili.+
19 “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo.+ Anthu anga amene anafa adzadzuka ndi kuimirira.+ Inu anthu okhala m’fumbi, dzukani, fuulani mokondwera!+ Pakuti mame anu+ ali ngati mame a maluwa,+ ndipo dziko lapansi lidzabereka anthu amene anafa.+
20 “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko.+ Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.+ 21 Pakuti taonani! Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala kuti adzaimbe mlandu anthu okhala m’dzikoli.+ Magazi amene dzikoli linakhetsa lidzawaonetsa poyera,+ ndipo silidzabisanso anthu amene linapha.”+
27 M’tsiku limenelo, Yehova+ adzagwiritsa ntchito lupanga lake lakuthwa,+ lalikulu ndi lochititsa mantha kupha Leviyatani,*+ njoka yokwawa mwamyaa!+ Ndithu adzapha Leviyatani, njoka yoyenda mothamanga ndi mokhotakhota, ndipo adzapha chinjoka chachikulu chokhala m’nyanja.+
2 M’tsiku limenelo anthu inu mudzaimbire mkaziyo+ kuti: “Iwe ndiwe munda wa mpesa+ wotulutsa vinyo wathovu. 3 Ine Yehova ndine mlonda wa mundawo.+ Ndizidzauthirira nthawi zonse.+ Ndizidzaulondera usana ndi usiku kuti wina aliyense asauwononge.+ 4 Ndaleka kumukwiyira.+ Munthu wina akaika zitsamba zaminga ndi udzu pamaso panga,+ ndidzazipondaponda ndi kuzitentha nthawi imodzi ndipo ndidzamenyana naye.+ 5 Apo ayi, iye athawire kumalo anga achitetezo. Akhazikitse mtendere ndi ine. Iye akhazikitse mtendere ndi ine.”+
6 M’masiku amene akubwerawo, Yakobo adzamera mizu n’kukhala wamphamvu ngati mtengo. Isiraeli+ adzakhala ngati mtengo waukulu wa maluwa ambiri. Iwo adzabereka zipatso panthaka ya dziko lonse lapansi.+
7 Kodi iye akufunikira kumenyedwa ngati mmene akumenyedweramu? Kapena kodi iye akufunikira kuphedwa ngati mmene anthu ake akuphedweramu?+ 8 Udzalimbana naye ndi mfuu yoopseza pomuthamangitsa. Iye adzamuthamangitsa ndi mphepo yake yamphamvu m’tsiku la mphepo ya kum’mawa.+ 9 Chotero zolakwa za Yakobo zidzaphimbidwa mwa njira imeneyi.+ Zimenezi zidzachitika akadzachotsa tchimo lakelo,+ ndiponso akadzasandutsa miyala yonse ya paguwa lansembe kukhala miyala yofewa kwambiri yonyenyekanyenyeka, moti mizati yopatulika+ ndi maguwa ofukizirapo zonunkhira sizidzamangidwanso.+ 10 Pakuti mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri udzatsala wokhawokha. Malo odyetserako ziweto adzakhala opanda kanthu ndipo adzasiyidwa ngati chipululu.+ Kumeneko mwana wa ng’ombe azidzadya msipu ndipo azidzagona pansi. Iye adzadya nthambi zake.+ 11 Tinthambi take tikadzauma, akazi obwera kumeneko adzatithyola n’kutiyatsa.+ Pakuti anthuwo si omvetsa zinthu.+ N’chifukwa chake yemwe anawapanga sadzawachitira chifundo, ndipo yemwe anawaumba sadzawakomera mtima.+
12 Inu ana a Isiraeli, monga momwe munthu amathyolera zipatso mumtengo n’kuzisonkhanitsa+ pamodzi chimodzi ndi chimodzi, Yehova adzakusonkhanitsani inu+ amene mwamwazikana m’dera loyambira ku Mtsinje*+ mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+ 13 M’tsiku limenelo kudzalira lipenga lomveka kutali.+ Ndiyeno anthu amene akuwonongeka m’dziko la Asuri+ ndi amene anamwazikana m’dziko la Iguputo,+ adzabwera kudzagwadira+ Yehova m’phiri loyera ku Yerusalemu.+
28 Tsoka kwa chisoti chaulemerero cha zidakwa za ku Efuraimu!+ Chisoticho changokhala ngati nkhata yamaluwa yokongola, imene maluwa ake akufota. Nkhata yamaluwayo yavalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde, kumene zidakwa zoledzera ndi vinyozo zimakhala. 2 Taonani! Yehova ali ndi winawake wamphamvu ndi wanyonga.+ Monga mvula yamabingu ndi yamatalala,+ mvula yamphepo yowononga, ndiponso monga mvula yamabingu ya madzi amphamvu osefukira,+ iye adzagwetsera pansi chisoti chaulemererocho mwamphamvu. 3 Zisoti zaulemerero za zidakwa za ku Efuraimu, zidzapondedwapondedwa ndi mapazi.+ 4 Nkhata yamaluwa yokongola imene maluwa ake akufota,+ yomwe ili pamwamba pa phiri m’chigwa chachonde, idzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kucha+ chilimwe chisanafike, imene munthu akaiona amaithyola n’kuimeza msangamsanga.
5 M’tsiku limenelo, Yehova wa makamu adzakhala ngati chisoti chokongoletsera+ ndiponso ngati nkhata yamaluwa yokongola+ kwa anthu ake otsala.+ 6 Adzakhalanso ngati mzimu wa chilungamo kwa munthu wopereka chiweruzo,+ ndiponso adzakhala ngati mphamvu kwa anthu opitikitsa adani amene afika pachipata kudzamenyana nawo.+
7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Ansembe ndi aneneri+ asochera chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Asokonezeka chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku+ chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Sakuonanso bwino ndipo zochita zawo zikusonyeza kuti sakuganiza bwino. 8 Pakuti matebulo onse adzaza masanzi.+ Paliponse pali masanzi okhaokha.
9 Kodi iyeyo akufuna aphunzitse ndani kudziwa zinthu,+ ndipo akufuna achititse ndani kumvetsetsa uthenga umene wanenedwa?+ Kodi ifeyo akutiyesa ana amene asiya kuyamwa, amene achotsedwa kubere?+ 10 Pakuti ndi “lamulo pa lamulo, lamulo pa lamulo, chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera, apa pang’ono, apo pang’ono.”*+ 11 Pakuti iye adzalankhula kwa anthu awa kudzera mwa anthu achibwibwi+ ndiponso olankhula lilime lachilendo,+ 12 anthu amene wawauza kuti: “Awa ndiye malo opumira. Pumitsani munthu wotopa. Amenewa ndiwo malo ampumulo,” koma amene sanafune kumva.+ 13 Kwa iwowo mawu a Yehova adzakhaladi “lamulo pa lamulo, lamulo pa lamulo, chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera,+ apa pang’ono, apo pang’ono,” kuti akagwe chagada n’kuthyoka, kukodwa ndi kugwidwa.+
14 Chotero imvani mawu a Yehova inu anthu odzitama, inu atsogoleri+ a anthu awa amene muli mu Yerusalemu: 15 Pakuti anthu inu mwanena kuti: “Ife tachita pangano ndi Imfa.+ Taona masomphenya limodzi ndi Manda.+ Ngati madzi osefukira atadutsa kuno, safika kwa ife pakuti bodza talisandutsa pothawirapo pathu,+ ndiponso tabisala m’chinyengo.”+ 16 Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikuika mwala mu Ziyoni+ kuti ukhale maziko. Umenewu ndi mwala+ wapakona woyesedwa,+ wamtengo wapatali,+ woti ukhale maziko olimba.+ Palibe munthu woukhulupirira amene adzade nkhawa.+ 17 Chilungamo+ ndidzachisandutsa chingwe choyezera+ ndipo ndidzachisandutsanso chipangizo chowongolera.* Mvula yamatalala+ idzakokolola malo othawirapo abodza + ndipo madzi adzasefukira pamalo obisalako.+ 18 Pangano lanu limene mwachita ndi Imfa lidzatha,+ ndipo masomphenya anu amene mwaona ndi Manda sadzagwira ntchito.+ Madzi osefukira akadzadutsa+ adzakukokololani.+ 19 Nthawi iliyonse imene akudutsa, azidzakutengani anthu inu+ chifukwa azidzadutsa m’mawa uliwonse. Azidzadutsanso usana ndi usiku ndipo adzangokhala chinthu chonjenjemeretsa,+ kuti ena amvetse uthenga umene wanenedwa.”
20 Pakuti bedi lafupika kwambiri moti munthu sangathe kugonapo mowongoka bwinobwino, ndipo nsalu yofunda yachepa kwambiri moti sikukwanira kuti munthu afunde bwinobwino. 21 Yehova adzaimirira monga mmene anachitira paphiri la Perazimu.+ Adzakalipa ngati mmene anachitira m’chigwa cha kufupi ndi Gibeoni+ kuti achite ntchito yake. Ntchito yakeyo ndi yodabwitsa. Adzakalipa kuti achite zochita zake. Zochita zakezo n’zachilendo.+ 22 Tsopano musakhale anthu onyoza+ chifukwa zingwe zanu zingakhale zolimba, pakuti ndamva kuchokera kwa Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ kuti dziko lonse laweruzidwa kuti liwonongedwe.+
23 Anthu inu tcherani khutu ndipo mvetserani mawu anga. Khalani tcheru ndipo mverani zonena zanga. 24 Kodi wolima munda ndi pulawo amangokhalira kulima nthawi zonse,+ kuphwanya zibuma, ndi kusalaza dothi, osabzala mbewu?+ 25 Kodi iye akasalaza dothilo si paja amawazapo chitowe chakuda ndiponso amafesapo chitowe chamtundu wina?+ Kodi si paja amabzalanso tirigu, mapira+ ndi balere m’malo ake,+ ndipo m’mphepete mwa mundawo+ amabzalamo mbewu zinanso?*+ 26 Mulungu amalangiza+ munthu moyenerera ndipo amam’phunzitsa.+ 27 Pakuti anthu sapuntha chitowe chakuda ndi chida chopunthira+ ndipo pachitowe chamtundu wina sayendetsapo mawilo a ngolo yopunthira mbewu. Nthawi zambiri chitowe chakuda amachipuntha ndi ndodo+ ndipo chitowe chamtundu wina amachipuntha ndi kamtengo. 28 Kodi tirigu amene ali popunthira mbewu, amamuphwanya? Munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo mosalekeza.+ Iye amayendetsa magudumu ake opunthira, ndi mahatchi ake, koma saphwanya tiriguyo.+ 29 Izi zachokeranso kwa Yehova wa makamu+ amene zolinga zake ndi zabwino kwambiri, ndiponso amene wachita zopambana kwambiri.+
29 “Tsoka kwa Ariyeli!*+ Tsoka kwa Ariyeli, tauni imene Davide anamangako msasa.+ Anthu inu, pitirizani kuchita zikondwerero+ zanu chaka ndi chaka. 2 Ariyeli ndidzamukhwimitsira zinthu,+ ndipo padzakhala kulira ndi kumva chisoni.+ Kwa ine, iye adzakhala ngati malo osonkhapo moto paguwa lansembe la Mulungu.+ 3 Ine ndidzamanga misasa mokuzungulira mbali zonse kuti ndichite nawe nkhondo. Ndidzamanga mpanda wa mitengo yosongoka mokuzungulira, ndipo ndidzamanga chiunda choti ndidzamenyerepo nkhondo pomenyana nawe.+ 4 Iweyo udzatsika moti uzidzalankhula uli pansi penipeni. Mawu ako azidzamveka otsika ngati akuchokera m’fumbi.+ Mawuwo adzachokera m’dothi ngati a wolankhula ndi mizimu, ndipo adzamveka ngati kulira kwa mbalame kuchokera m’fumbi.+ 5 Khamu la anthu achilendo lidzasanduka fumbi losalala,+ ndipo khamu la olamulira ankhanza+ lidzakhala ngati mankhusu amene akuuluzika.+ Zimenezi zidzachitika mwadzidzidzi, mosayembekezereka.+ 6 Yehova wa makamu adzatembenukira kwa iwe kuti akupulumutse ndi mabingu, zivomezi, phokoso lalikulu, mphepo yamkuntho, ndi lawi la moto wowononga.”+
7 Khamu la mitundu yonse imene ikuchita nkhondo ndi Ariyeli,+ onse amene akumenyana naye ndi kumumangira nsanja zomenyerapo nkhondo, ndiponso amene akumukhwimitsira zinthu,+ adzaona ngati za m’maloto, za m’masomphenya a usiku. 8 Inde, zidzawachitikira ngati pamene munthu wanjala akulota kuti akudya, kenako n’kudzidzimuka n’kuona kuti m’mimba mwake mulibe kanthu,+ kapena ngati pamene munthu waludzu akulota kuti akumwa madzi, n’kudzidzimuka n’kuona kuti adakali wotopa ndipo kukhosi kwake n’kouma. Umu ndi mmene zidzachitikire ndi khamu lonse la mitundu imene ikuchita nkhondo ndi phiri la Ziyoni.+
9 Anthu inu, dabwani ndipo chitani kukamwa yasa!+ Matani maso anu kuti musaone.+ Iwo aledzera,+ koma osati ndi vinyo. Akudzandira, koma osati chifukwa cha chakumwa choledzeretsa.+
10 Pakuti Yehova wakukhuthulirani mzimu wa tulo tatikulu+ ndipo watseka maso anu, omwe ndi aneneri.+ Waphimba mitu yanu,+ imene ndi anthu amasomphenya.+ 11 Kwa anthu inu, masomphenya a chilichonse akhala ngati mawu a m’buku limene lamatidwa kuti lisatsegulidwe,+ limene alipereka kwa munthu wodziwa kuwerenga, n’kumuuza kuti: “Werenga bukuli mokweza.” Koma iye n’kunena kuti: “Sindingathe kuliwerenga, chifukwa ndi lomatidwa.”+ 12 Kenako bukulo laperekedwa kwa munthu wosadziwa kuwerenga, n’kumuuza kuti: “Werenga bukuli mokweza,” koma iye n’kuyankha kuti: “Sindidziwa kuwerenga m’pang’ono pomwe.”
13 Yehova wanena kuti: “Popeza anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha+ koma mtima wawo auika kutali ndi ine,+ ndiponso amangophunzira malamulo a anthu n’kumaganiza kuti kuchita zimenezo ndiye kundiopa,+ 14 ine ndidzachitanso zodabwitsa ndi anthu awa.+ Ndidzazichita m’njira yodabwitsa, pogwiritsira ntchito chinthu chodabwitsa. Nzeru za anthu awo anzeru zidzatha, ndipo kumvetsetsa zinthu kwa anthu awo ozindikira kudzabisika.”+
15 Tsoka kwa anthu amene abisa patali kwambiri zolinga zawo, pozibisira Yehova,+ amene zochita zawo zimachitikira m’malo a mdima,+ ndipo amati: “Ndani akutiona, ndipo ndani akudziwa zimene tikuchita?”+ 16 Anthu inu ndinu opotoka maganizo kwabasi! Kodi woumba zinthu ndi dongo angafanane ndi dongolo?+ Kodi chinthu chochita kupangidwa chingamunene amene anachipanga, kuti: “Iye uja sanandipange”?+ Komanso kodi chinthu chochita kuumbidwa chingamunene amene anachiumba, kuti: “Iye uja sanasonyeze kuti ndi womvetsa zinthu”?+
17 Kodi si pangotsala kanthawi kochepa kuti Lebanoni asanduke munda wa zipatso,+ ndiponso kuti munda wa zipatsowo udzangokhala ngati nkhalango?+ 18 M’tsiku limenelo, ogontha adzamva mawu a m’buku.+ Ngakhale maso a anthu akhungu adzamasuka ku mdima wandiweyani ndipo adzayamba kuona.+ 19 Ofatsa+ adzawonjezera kukondwa mwa Yehova, ndipo ngakhale osauka pakati pa anthu adzasangalala ndi Woyera wa Isiraeli,+ 20 chifukwa wolamulira wankhanza adzafika pamapeto pake,+ ndipo wodzitama adzatha.+ Onse okhala tcheru kuti achitire anzawo zoipa+ adzaphedwa, 21 amene amachimwitsa munthu ndi mawu ake,+ amene amatchera msampha munthu wodzudzula ena pachipata,+ ndiponso amene amagwiritsira ntchito mfundo zopanda umboni pokankhira pambali munthu wolungama.+
22 Chotero Yehova, amene anawombola Abulahamu, wanena izi kwa nyumba ya Yakobo:+ “Tsopano Yakobo sachita manyazi. Tsopano nkhope yake sikhala yakugwa,+ 23 pakuti akaona ana ake pakati pake, ntchito ya manja anga,+ iwo adzayeretsa dzina langa.+ Adzayeretsadi Woyera wa Yakobo,+ ndipo adzalemekeza kwambiri Mulungu wa Isiraeli.+ 24 Anthu amene akuganiza molakwa mumtima mwawo adzamvetsa zinthu, ndipo ngakhale amene akudandaula adzalandira malangizo.”+
30 Yehova wanena kuti: “Tsoka kwa ana aamuna osamva,+ amene amakonda kuchita zofuna zawo osati zofuna zanga,+ amene amapanga mgwirizano mwa kuthira pansi chakumwa monga nsembe motsutsana ndi zofuna zanga,* kuti awonjezere tchimo pa tchimo,+ 2 amene akupita ku Iguputo+ osafunsira kwa ine,+ ndiponso amene akupita ku Iguputo kuti akapeze chitetezo kwa Farao ndi kukabisala mumthunzi wa Iguputo.+ 3 Chitetezo cha Farao chidzakhala chochititsa manyazi kwa amuna inu,+ ndipo kubisala mumthunzi wa Iguputo kudzakhala chinthu chopereka chitonzo.+ 4 Pakuti akalonga ake afika ku Zowani,+ ndipo nthumwi zake zafika mpaka ku Hanesi. 5 Aliyense adzachita manyazi ndi anthu opanda phindu, osathandiza ndi osapindulitsa, omwe ndi ochititsa manyazi ndi otonzetsa.”+
6 Uwu ndi uthenga wokhudza zilombo zokhala kum’mwera:+ Podutsa m’dziko lamavuto+ ndi la zowawa, la mikango ndi kulira kwa akambuku, la mphiri ndi la njoka zothamanga zaululu wamoto,+ iwo anyamulira chuma chawo pamsana pa abulu akuluakulu.+ Anyamuliranso katundu wawo pamalinunda a ngamila. Koma zinthu zimenezi zidzakhala zopanda phindu kwa anthu amenewa. 7 Aiguputo ndi anthu achabechabe ndipo sadzakuthandizani chilichonse.+ Choncho ndinawatcha kuti, “Rahabi.+ Iwo sadzachita chilichonse.”
8 “Tsopano lemba zimenezi pacholembapo, iwo akuona. Uzilembe m’buku+ kuti m’tsogolo zidzakhale umboni mpaka kalekale.+ 9 Pakuti amenewa ndi anthu opanduka,+ ana ochita zachinyengo,+ amene safuna kumva malamulo a Yehova,+ 10 amene auza anthu oona masomphenya kuti: ‘Lekani kuona masomphenya,’ ndipo anthu olosera zam’tsogolo awauza kuti: ‘Musamalosere zoona zokhudza ife.+ Muzilankhula kwa ife zabwino zokhazokha. Muziona masomphenya abodza.+ 11 Patukani panjira. Dzerani njira ina.+ Musatiuzenso za Woyera wa Isiraeli.’”+
12 Chotero Woyera wa Isiraeli wanena kuti: “Anthu inu mwakana mawu anga+ n’kumadalira kuba mwachinyengo. Mukudalira zinthu zachinyengo ndipo mukukhulupirira zinthu zimenezo.+ 13 Pa chifukwa chimenechi, kwa inu cholakwa chanuchi chidzakhala ngati mpanda wautali kwambiri umene wang’aluka penapake n’kupendekeka,+ umene ukhoza kugwa mwadzidzidzi, mosayembekezereka.+ 14 Munthu adzaugwetsa ngati mmene amaphwanyira mtsuko waukulu wadothi,+ mtsukowo n’kuphwanyikiratu wonse n’kungokhala tizidutswatizidutswa, ndipo patizidutswapo osapezeka ngakhale phale loti n’kupalira moto kapena kutungira madzi padambo.”+
15 Pakuti Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Anthu inu mukabwerera kwa ine n’kusiya zimene mukuchita, mudzapulumuka. Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”+ Koma inu simunafune.+ 16 Ndipo munanena kuti: “Ayi, ife tidzakwera pamahatchi n’kuthawa!”+ N’chifukwa chake mudzathawe. Munanenanso kuti: “Tidzakwera pamahatchi othamanga kwambiri!”+ N’chifukwa chake anthu okuthamangitsani adzakhale othamanga kwambiri.+ 17 Anthu 1,000 adzanjenjemera chifukwa cha mawu oopseza a munthu mmodzi.+ Ndipo chifukwa cha mawu oopseza a anthu asanu, inuyo mudzathawa mpaka mudzatsala ochepa ngati mtengo wautali wa pangalawa wozikidwa pamwamba pa phiri, ndiponso ngati mtengo wozikidwa pamwamba pa phiri laling’ono kuti ukhale chizindikiro.+
18 Chotero Yehova azidzayembekezera kuti akukomereni mtima+ ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo,+ pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo.+ Odala+ ndi anthu onse amene amamuyembekezera.+ 19 Anthu a ku Ziyoni+ akadzabwerera n’kukakhala ku Yerusalemu,+ iwe sudzaliranso.+ Mosakayikira, iye adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako. Akadzangomva kulira kwakoko, iye adzakuyankha.+ 20 Yehova adzakupatsani masautso kuti akhale chakudya chanu, ndiponso adzakupatsani kuponderezedwa kuti kukhale madzi anu akumwa.+ Koma Mlangizi wako Wamkulu adzasiya kudzibisa ndipo maso ako adzayamba kuona Mlangizi wako Wamkulu.+ 21 Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwako, akuti: “Njira ndi iyi.+ Yendani mmenemu anthu inu.” Yendani m’njira imeneyi kuti musasochere n’kulowera kudzanja lamanja kapena lamanzere.+
22 Zophimbira mafano anu ogoba asiliva ndi zokutira zifaniziro zanu zopangidwa ndi golide+ wosungunula,+ mudzaziona kuti ndi zonyansa+ ndipo mudzazitaya.+ Monga mkazi amene akusamba yemwe amataya monyansidwa kansalu kake, mudzanena kuti: “Nyansi zimenezi!”+ 23 Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munabzala munthaka,+ ndipo zokolola za munthakayo zidzakhala chakudya chopatsa thanzi.+ M’tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+ 24 Ng’ombe ndi abulu akuluakulu olima, zidzadya chakudya chokoma chosakaniza ndi zitsamba zowawasira, chimene mankhusu ake anauluzidwa pogwiritsa ntchito fosholo+ ndi chifoloko. 25 M’tsiku limene anthu ambiri adzaphedwe ndiponso limene nsanja zidzagwe, paphiri lililonse lalitali ndi paphiri lililonse laling’ono padzakhala timitsinje+ ndi ngalande zamadzi.+ 26 Kuwala kwa mwezi wathunthu kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa lowala kwambiri. Kuwala kwa dzuwa lowala kwambiri kudzawonjezereka maulendo 7+ ndipo kudzakhala ngati kuwala kwa masiku 7. Zimenezi zidzachitika m’tsiku limene Yehova adzachiritse mtundu wake wovulala+ ndi kupoletsa+ chilonda choopsa cha anthu ake, amene iyeyo anawavulaza powalanga.
27 Taonani! Dzina la Yehova likubwera kuchokera kutali. Likubwera ndi mkwiyo woyaka+ ndiponso mitambo yolemera. Pamilomo yake padzaza mawu odzudzula ndipo lilime lake lili ngati moto wowononga.+ 28 Mzimu wa Mulungu uli ngati mtsinje wosefukira umene wafika m’khosi,+ umene iye adzaugwiritsire ntchito posefa+ mitundu ya anthu monga zinthu zopanda pake. Pakamwa pa mitunduyo adzamangapo zingwe ngati zowongolera hatchi,+ zimene zidzawachititse kuyenda uku ndi uku.+ 29 Anthu inu mudzaimba nyimbo,+ ngati imene imaimbidwa usiku umene munthu amadziyeretsa pokonzekera chikondwerero.+ Mudzakhalanso ndi chimwemwe mumtima ngati munthu amene akuimba chitoliro+ popita kuphiri la Yehova,+ Thanthwe la Isiraeli.+
30 Yehova adzapangitsa kuti ulemerero wa mawu ake+ umveke. Adzapangitsa kuti dzanja lake limene likutsika lionekere.+ Dzanjalo lidzatsika ndi mkwiyo waukulu,+ lawi la moto wowononga,+ mvula yamphamvu ndiponso yamkuntho+ ndi matalala.+ 31 Chifukwa cha mawu a Yehova, dziko la Asuri lidzagwidwa ndi mantha,+ ndipo iye adzalimenya ndi ndodo.+ 32 Ulendo uliwonse umene Yehova adzakwapule Asuri ndi ndodo yake, kudzamveka kulira kwa maseche ndi azeze.+ Pomenyana nawo, iye azidzazunguza zida zake uku ndi uku.+ 33 Malo otchedwa Tofeti*+ owonongerako Asuri akonzedwa kale. Malowo akonzedweranso mfumu yawo.+ Malo amene iye wakonzawo ndi ozama ndipo kuli moto waukulu ndi nkhuni zambiri. Mpweya wa Yehova ukuyatsa malowo ngati mtsinje wa sulufule.+
31 Tsoka kwa anthu amene akupita ku Iguputo kukapempha thandizo.+ Iwo akudalira mahatchi wamba+ ndi kukhulupirira magaleta ankhondo,+ chifukwa chakuti ndi ambiri. Akudaliranso mahatchi akuluakulu chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri, koma sanayang’ane kwa Woyera wa Isiraeli ndipo sanafunefune Yehova.+ 2 Iyenso ndi wanzeru+ ndipo adzabweretsa tsoka.+ Sadzabweza mawu ake+ ndipo adzaukira nyumba ya anthu ochita zoipa.+ Adzalepheretsa anthu amene amachita zopweteka anzawo, kupeza chithandizo chimene amafuna.+
3 Koma Aiguputowo ndi anthu ochokera kufumbi.+ Si Mulungu ayi. Mahatchi awo ndi zinyama,+ osati mzimu. Yehova akadzatambasula dzanja lake, amene akupereka thandizo adzapunthwa, ndipo amene akuthandizidwawo adzagwa.+ Onsewo adzatha nthawi imodzi.
4 Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Mkango umalira moopseza, ngakhale mkango wamphamvu,+ poteteza nyama imene wagwira. Abusa ambirimbiri akaitanidwa kuti adzauthamangitse, ngakhale umve mawu awo suchita mantha ndipo ngakhale azichita phokoso suopa. M’njira yomweyo, Yehova wa makamu adzatsika kuti achite nkhondo poteteza phiri la Ziyoni ndiponso poteteza phiri lake laling’ono.+ 5 Monga imachitira mbalame imene ikuuluka kuti iteteze ana ake, Yehova wa makamu adzateteza mzinda wa Yerusalemu.+ Iye adzauteteza n’kuupulumutsa.+ Adzausunga n’kuuthandiza kuti upulumuke.”
6 “Inu ana a Isiraeli, bwererani+ kwa amene mwamupandukira ndi kumulakwira kwambiri.+ 7 Pakuti m’tsiku limenelo, aliyense wa inu adzataya milungu yake yasiliva yachabechabe, ndi milungu yake yagolide yopanda phindu,+ imene manja anu akupangirani n’kukuchimwitsani nayo.+ 8 Msuri adzaphedwa ndi lupanga, koma osati la munthu. Lupanga lidzamudya, koma osati la munthu wochokera kufumbi.+ Iye adzathawa chifukwa cha lupangalo ndipo ana ake aamuna adzagwiritsidwa ntchito yaukapolo. 9 Thanthwe lake lidzachoka chifukwa cha mantha ndipo akalonga ake adzachita mantha chifukwa cha chizindikiro,”+ akutero Yehova, amene kuwala kwake kuli mu Ziyoni ndiponso amene ng’anjo+ yake ili mu Yerusalemu.
32 Taonani! Mfumu+ idzalamulira mwachilungamo,+ ndipo akalonga+ adzalamuliranso mwachilungamo. 2 Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho,+ ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi,+ ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.+
3 Maso a anthu otha kuona sadzatsekeka, ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsera mwatcheru.+ 4 Mtima wa anthu opupuluma udzafunafuna kudziwa zinthu,+ ndipo ngakhale lilime la anthu achibwibwi lidzalankhula bwinobwino zinthu zomveka.+ 5 Munthu wopusa sadzatchedwanso wopatsa, ndipo munthu wopanda khalidwe sadzatchedwa wolemekezeka,+ 6 pakuti munthu wopusa adzalankhula zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mtima wake udzaganiza zochita zinthu zopweteka ena.+ Iye adzachita zimenezi kuti azichita zopanduka,+ kuti azinenera Yehova zoipa, kuti achititse mimba ya munthu wanjala kukhala yopanda kanthu,+ ndiponso kuti achititse munthu waludzu kukhala wopanda chilichonse choti amwe. 7 Munthu wakhalidwe loipayo, njira zake n’zoipa.+ Iye amakonza zochita khalidwe lotayirira,+ n’cholinga choti apweteke anthu ozunzika pogwiritsa ntchito mawu abodza,+ ngakhale pamene munthu wosauka akunena zoona.
8 Koma munthu wopatsa amapereka malangizo okhudza kupatsa, ndipo iyeyo amapitiriza kukhala wopatsa.+
9 “Inu akazi amene mukukhala mosatekeseka, nyamukani! Mvetserani mawu anga!+ Inu ana aakazi osasamala, mverani zimene ndikunena! 10 Pomatha chaka ndi masiku angapo, anthu osasamalanu mudzatekeseka,+ chifukwa ngakhale nyengo yokolola mphesa itatha, sipadzakhala mphesa zilizonse zimene zasonkhanitsidwa.+ 11 Inu akazi amene mukukhala mosatekeseka, njenjemerani! Inu osasamala, chitani mantha! Vulani n’kukhala maliseche, ndipo muvale ziguduli m’chiuno mwanu.+ 12 Dzimenyeni pachifuwa pomva chisoni+ chifukwa cha kuwonongeka kwa minda yachonde+ ndi minda ya mpesa. 13 Panthaka ya anthu anga, pakungomera zitsamba zaminga.+ Zamera panyumba zonse zimene kale zinali zodzaza ndi chisangalalo. Zamera m’tauni imene kale inali yodzaza ndi chikondwerero.+ 14 Pakuti nsanja yokhalamo yasiyidwa,+ piringupiringu amene anali mumzindamo watha. Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka tchire. Mpaka kalekale zidzakhala malo osangalalako mbidzi, ndi odyetserako ziweto, 15 kufikira mzimu utatsanulidwa pa ife kuchokera kumwamba,+ ndiponso chipululu chitakhala munda wa zipatso. Munda wa zipatsowo udzakhala ngati nkhalango yeniyeni.+
16 “M’chipululumo mudzakhala chilungamo, ndiponso m’munda wa zipatsowo mudzakhala chilungamo.+ 17 Ntchito ya chilungamo chenicheni idzakhala mtendere,+ ndipo zochita za chilungamo chenicheni zidzakhala bata ndi mtendere mpaka kalekale.+ 18 Anthu anga adzakhala pamalo amtendere ndi pamalo otetezeka. Adzakhala m’malo abata ndiponso aphee!+ 19 Kudzagwa matalala nkhalango ikadzatha,+ ndiponso mzinda ukadzatsitsidwa n’kukhala wonyozeka.+
20 “Odala ndinu anthu amene mukubzala mbewu m’mphepete mwa madzi onse,+ ndi kumasula ng’ombe yamphongo ndi bulu.”+
33 Tsoka iwe amene ukulanda zinthu koma iweyo osalandidwa. Tsoka kwa iwe amene ukuchita zachinyengo pamene ena sanakuchitire zachinyengo.+ Ukadzangomaliza kulanda, nawenso udzalandidwa.+ Ukadzangomaliza kuchitira ena zachinyengo, iwonso adzakuchitira zachinyengo.+
2 Inu Yehova, tikomereni mtima.+ Ife tikudalira inu.+ Tilimbitseni ndi dzanja lanu+ m’mawa uliwonse.+ Mukhale chipulumutso chathu pa nthawi ya masautso.+ 3 Mitundu ya anthu yathawa itamva mkokomo wa mawu anu.+ Mitundu yamwazikana chifukwa chakuti inu mwanyamuka.+ 4 Zinthu zimene anthu inu munalanda+ ena zidzasonkhanitsidwa ngati mphemvu zikasonkhana pamodzi, ndiponso ngati chigulu cha dzombe chimene chikukhamukira kwa munthu.+ 5 Yehova adzakwezedwa pamwamba,+ pakuti amakhala pamalo apamwamba.+ Iye adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo.+ 6 M’masiku anu, kukhulupirika kudzabweretsa chipulumutso chachikulu.+ Nazonso nzeru, kudziwa zinthu,+ ndi kuopa Yehova,+ komwe ndiko chuma chake zidzabweretsa chipulumutso chachikulu.
7 Ndipotu anthu awo otchuka adzalira mofuula m’misewu. Amithenga a mtendere+ adzalira momvetsa chisoni. 8 Misewu ikuluikulu yawonongeka.+ Palibenso munthu woyenda m’njira.+ Iye waphwanya pangano+ ndipo wanyansidwa ndi mizinda.+ Sasamala za munthu aliyense.+ 9 Dzikolo likulira, lafota.+ Lebanoni wachita manyazi, wanyala.+ Sharoni+ wakhala ngati chipululu ndipo Basana ndi Karimeli akuyoyola masamba awo.+
10 Yehova wati: “Tsopano ndinyamuka,+ ndidzikweza.+ Tsopano ndidziika pamwamba.+ 11 Anthu inu muli ndi pakati pa udzu wouma+ ndipo mudzabereka mapesi. Mzimu wanu udzakunyeketsani+ ngati moto.+ 12 Mitundu ya anthu idzakhala ngati zotsala za laimu akatenthedwa. Iwo adzayaka ndi moto ngati minga zimene zasadzidwa.+ 13 Anthu inu amene muli kutali, imvani zimene ndikufuna kuchita.+ Inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga.+ 14 Mu Ziyoni, anthu ochimwa akuchita mantha.+ Opanduka akunjenjemera kwambiri.+ Akufunsa kuti: ‘Ndani wa ife angakhale pambali pa moto wowononga?+ Ndani wa ife angakhale pafupi ndi moto woyaka kwambiri wosatherapo?’+
15 “Pali munthu amene amayenda m’chilungamo nthawi zonse,+ amene amalankhula zowongoka,+ amene amakana kupeza phindu mwachinyengo,+ amene salola kuti manja ake alandire chiphuphu,+ amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi, ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zoipa.+ 16 Iye ndi amene adzakhale pamalo apamwamba.+ Malo ake okhala adzakhala otetezeka m’matanthwe movuta kufikamo.+ Iye adzapatsidwa chakudya+ ndipo madzi ake sadzatha.”+
17 Maso ako adzaona kukongola kwa mfumu.+ Adzaona dziko lakutali.+ 18 Mtima wako udzalankhula motsitsa mawu+ za chinthu choopsa kuti: “Kodi mlembi ali kuti? Kodi wopereka malipiro uja ali kuti?+ Uja amawerenga nsanjayu ali kuti?”+ 19 Simudzaona anthu achipongwe, amene chilankhulo chawo n’chovuta kumva, anthu achibwibwi olankhula zinthu zovuta kumva.+ 20 Taonani Ziyoni,+ tauni yathu yochitiramo zikondwerero.+ Maso anu adzaona Yerusalemu, amene ndi malo okhala aphee, opanda chosokoneza chilichonse. Iye ndi hema woti palibe amene adzamuchotse.+ Zikhomo zake sizidzazulidwa ndipo zingwe zake sizidzaduka.+ 21 Koma kumeneko, Yehova Wolemekezeka+ adzakhala malo a mitsinje+ ndi a ngalande zikuluzikulu kwa ife. Kumalo amenewo sikudzadutsa gulu la ngalawa kapena zombo zikuluzikulu. 22 Pakuti Yehova ndiye Woweruza wathu.+ Yehova ndiye Wotipatsa Malamulo.+ Yehova ndiye Mfumu yathu.+ Iye adzatipulumutsa.+
23 Zingwe zidzakhala zosamanga. Mtengo wautali wa pangalawa sadzatha kuuimika mowongoka. Chinsalu chapangalawayo sadzatha kuchitambasula.
Pa nthawi imeneyo adzagawana zofunkha zambirimbiri. Ngakhale anthu olumala adzatenga nawo katundu wambiri wofunkha.+ 24 Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: “Ndikudwala.”+ Anthu okhala mmenemo adzakhala amene machimo awo anakhululukidwa.+
34 Mitundu inu, bwerani pafupi kuti mumve.+ Inu mitundu ya anthu,+ mvetserani. Dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo zimvetsere.+ Nthaka ya padziko lapansi+ ndi zonse zimene zili pamenepo zimve.+ 2 Pakuti Yehova wakwiyira mitundu yonse.+ Wapsera mtima asilikali awo onse.+ Iye awawononga ndipo awapha.+ 3 Anthu awo ophedwa adzatayidwa, ndipo fungo loipa la mitembo yawo lidzakwera m’mwamba.+ Mapiri adzasungunuka chifukwa cha magazi awo.+ 4 Makamu onse akumwamba adzawola.+ Kumwamba kudzapindidwa ngati mpukutu wolembapo.+ Makamu onse akumwambawo adzafota ngati mmene masamba amafotera pamtengo wa mpesa n’kuthothoka, ndiponso ngati mmene nkhuyu yonyala imathothokera mumtengo wa mkuyu.+
5 “Pakuti lupanga langa+ lidzakhala magazi okhaokha kumwambako. Lupangalo lidzatsikira pa Edomu+ ndi pa anthu amene ndikufuna kuwawononga+ mogwirizana ndi chilungamo changa. 6 Yehova ali ndi lupanga. Lupangalo lidzakhala magazi okhaokha+ ndipo lidzaterera ndi mafuta. Lidzadzaza magazi a nkhosa zamphongo zing’onozing’ono ndi a mbuzi zamphongo. Lidzaterera ndi mafuta+ a impso za nkhosa zamphongo, pakuti Yehova adzapereka nsembe ku Bozira ndipo adzapha nyama zambiri m’dziko la Edomu.+ 7 Ng’ombe zamphongo zam’tchire+ zidzatsetserekera nawo kumeneko, zing’onozing’ono ndi zamphamvu zomwe.+ Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha, ndipo fumbi lawo lidzanona ndi mafuta.”+
8 Pakuti Yehova ali ndi tsiku lobwezera adani ake,+ ndi chaka chopereka chilango, chifukwa cha zolakwa zimene Ziyoni anachitiridwa.+
9 Mitsinje yake* idzasintha n’kukhala phula. Fumbi lake lidzakhala sulufule, ndipo dziko lake lidzakhala ngati phula loyaka moto.+ 10 Usana ndi usiku, motowo sudzazima. Utsi wake uzidzakwera m’mwamba mpaka kalekale.+ Dzikolo lidzakhala louma ku mibadwomibadwo.+ Mpaka muyaya palibe amene adzadutseko.+ 11 Mbalame zotchedwa vuwo ndi nungu zidzakhala kumeneko. Komanso akadzidzi a makutu ataliatali ndi akhwangwala azidzakhala kumeneko.+ Iye adzatambasulira dzikolo chingwe choyezera+ malo opanda kanthu, ndiponso miyala yoyezera kuwongoka kwa chinthu. 12 Palibe aliyense wochokera pa anthu ake olemekezeka amene adzakhale mfumu, ndipo akalonga ake onse adzatha.+ 13 Minga zidzamera pansanja zake zokhalamo. Zomera zoyabwa ndi zitsamba zaminga zidzamera pamalo ake otetezeka,+ ndipo iye adzakhala malo okhala mimbulu+ ndi bwalo la nthiwatiwa.+ 14 Nyama zokhala kumadera opanda madzi zidzakumana ndi nyama zolira mokuwa, ndipo ngakhale ziwanda zooneka ngati mbuzi,*+ zizidzaitanizana kumeneko. Mbalame yotchedwa lumbe izidzasangalalako n’kupezako malo okhala.+ 15 Kumeneko, njoka yodumpha idzakonzako chisa chake n’kuikira mazira. Idzakhalira mazirawo n’kuswa tiana, ndipo idzatisonkhanitsa pansi pa mthunzi wake. Mbalame zotchedwa akamtema+ zidzasonkhana kumeneko iliyonse ndi mwamuna wake.
16 Fufuzani m’buku+ la Yehova ndipo muwerenge mokweza. Palibe ndi imodzi yomwe imene ikusowekapo.+ Zonsezo sizilephera kupeza mwamuna, chifukwa pakamwa pa Yehova ndi pamene palamula.+ Mzimu wake ndi umene wazisonkhanitsa pamodzi.+ 17 Iye ndi amene waziponyera maere, ndipo dzanja lake lazigawira malowo ndi chingwe choyezera.+ Zidzakhala kumeneko mpaka kalekale. Kudzakhala kwawo ku mibadwomibadwo.
35 Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala.+ Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.+ 2 Deralo lidzachitadi maluwa.+ Lidzasangalala ndipo lidzakondwera n’kufuula ndi chisangalalo.+ Lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni+ ndi kukongola kwa Karimeli+ ndiponso kwa Sharoni.+ Padzakhala anthu amene adzaone ulemerero wa Yehova+ ndi kukongola kwa Mulungu wathu.+
3 Anthu inu limbitsani manja ofooka ndiponso mawondo agwedegwede.+ 4 Amene ali ndi nkhawa mumtima mwawo muwauze kuti:+ “Limbani mtima.+ Musachite mantha.+ Pakuti Mulungu wanu adzabwera n’kudzabwezera adani anu.+ Mulungu adzabwezera chilango.+ Iye adzabwera n’kukupulumutsani.”+
5 Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa,+ ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva.+ 6 Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.+ Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.+ Pakuti m’chipululu mudzatumphuka madzi ndipo m’dera lachipululu mudzayenda mitsinje. 7 Malo ouma chifukwa cha kutentha adzakhala dambo la madzi, ndipo malo aludzu adzakhala malo a akasupe amadzi.+ Kumalo okhala mimbulu,+ malo ake ousako, kudzakhala udzu wobiriwira, mabango ndi gumbwa.+
8 Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+ ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero.+ Munthu wodetsedwa sadzayendamo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera. Palibe anthu opusa amene azidzayendayendamo. 9 Kumeneko sikudzakhala mkango ndipo nyama zolusa zakutchire sizidzafikako.+ Nyama zotere sizidzapezekako.+ Anthu ogulidwanso adzayenda mumsewuwo.+ 10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+
36 M’chaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera kudzachita nkhondo ndi mizinda yonse ya Ayuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo.+ 2 Pomalizira pake mfumu ya Asuri inatuma Rabisake*+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu.+ Inamutumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu. Iye anakaima pangalande+ yochokera kudziwe lakumtunda,+ pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+ 3 Kenako kunabwera Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu, Sebina+ mlembi, ndi Yowa+ mwana wa Asafu+ wolemba zochitika.+
4 Choncho Rabisake anawauza kuti: “Mukauze Hezekiya kuti, ‘Mfumu yaikulu,+ mfumu ya Asuri+ yanena kuti: “Kodi ukudalira chiyani?+ 5 Iwe wanena kuti (koma ndi mawu a pakamwa chabe), ‘Ine ndili ndi nzeru ndi mphamvu zofunika pankhondo.’+ Kodi ukudalira ndani popandukira ine?+ 6 Ukudalira thandizo la Iguputo,+ bango lophwanyika loti munthu ataligwira kuti limuchirikize,+ lingamucheke m’manja. Umu ndi mmene Farao+ mfumu ya Iguputo alili kwa onse omudalira.+ 7 Ngati inu mungandiuze kuti, ‘Tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si iye amene Hezekiya wamuchotsera malo ake okwezeka+ ndi maguwa ake ansembe,+ n’kuuza Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzigwada pamaso pa guwa lansembe ili’?”’+ 8 Tsopano ubetcherane+ ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri,+ ndipo ine ndikupatsa mahatchi 2,000 kuti ndione ngati iweyo ungathe kupeza okwerapo.+ 9 Kodi ungathe bwanji kubweza bwanamkubwa mmodzi, yemwe ndi mtumiki wotsika kwambiri wa mbuye wanga,+ pamene iweyo ukuchita kudalira Iguputo kuti akupatse magaleta ndi okwera pamahatchi?+ 10 Kodi ukuganiza kuti ndabwera kudzawononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova weniweniyo wandiuza kuti,+ ‘Pita ukamenyane ndi dzikolo, ndipo ukaliwononge.’”+
11 Pamenepo Eliyakimu,+ Sebina,+ ndi Yowa+ anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu m’chilankhulo cha Asiriya+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe m’chilankhulo cha Ayuda,+ kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.”+ 12 Koma Rabisake anayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene mawuwa kwa mbuye wanu yekha ndi kwa inuyo? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, kuti adye chimbudzi chawo ndi kumwa mkodzo wawo limodzi nanu?”+
13 Choncho Rabisake akadali chiimire,+ anapitiriza kulankhula mokweza m’chilankhulo cha Ayuda,+ kuti: “Imvani mawu a mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri.+ 14 Mfumuyo yanena kuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni anthu inu,+ chifukwa sangathe kukulanditsani.+ 15 Musalole kuti Hezekiya akuchititseni kudalira Yehova,+ pokuuzani kuti: “Mosakayikira Yehova atilanditsa,+ ndipo mzindawu superekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 16 Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Ndigonjereni,+ ndipo bwerani kwa ine. Aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu,+ komanso aliyense azimwa madzi a m’chitsime chake,+ 17 kufikira ine nditabwera kudzakutengerani kudziko lofanana ndi dziko lanulo.+ Ndidzakutengerani kudziko la mbewu ndi la vinyo watsopano, dziko la mkate ndi minda ya mpesa. 18 Musamvere Hezekiya chifukwa akukunyengererani+ ndi mawu akuti, ‘Yehova atilanditsa.’ Kodi pali mulungu wa mitundu ina amene wakwanitsa kupulumutsa mtundu wake m’manja mwa mfumu ya Asuri?+ 19 Kodi milungu ya Hamati+ ndi Aripadi+ ili kuti? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu?+ Kodi yalanditsa Samariya m’manja mwanga?+ 20 Ndi mulungu uti pakati pa milungu yonse ya mayiko amenewa, amene walanditsa dziko lake m’manja mwanga,+ kuti Yehova athe kulanditsa Yerusalemu m’manja mwanga?”’”+
21 Anthuwo anangokhala chete osamuyankha,+ chifukwa lamulo lochokera kwa mfumu linali lakuti: “Musamuyankhe.”+ 22 Koma Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu,+ Sebina+ mlembi, ndi Yowa+ mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kwa Hezekiya atang’amba zovala zawo+ n’kumuuza mawu a Rabisake.+
37 Mfumu Hezekiya itangomva zimenezi, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli.+ Kenako inapita m’nyumba ya Yehova.+ 2 Komanso inatuma Eliyakimu+ amene anali woyang’anira banja la mfumu, Sebina mlembi,+ ndi akuluakulu a ansembe,+ onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+ 3 Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa+ ndi lodzudzula, tsiku la mnyozo ndi mwano.+ Tili ngati mkazi amene watsala pang’ono kubereka, koma alibe mphamvu zoti aberekere.+ 4 Mwina Yehova Mulungu amva mawu onse a Rabisake,+ amene mbuye wake mfumu ya Asuri yamutuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira amene alipo.’”+
5 Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.+ 6 Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki+ a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza. 7 Ndiika maganizo+ mwa iye, kuti akamva nkhani inayake,+ abwerere kudziko lake. Ndipo mosalephera, ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga m’dziko lake.”’”+
8 Rabisake+ anali atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi,+ choncho anabwerera kwa mfumuyo n’kukaipeza ikumenyana ndi Libina.+ 9 Tsopano mfumuyo inamva kuti Tirihaka+ mfumu ya Itiyopiya wabwera kudzamenyana nayo. Itangomva zimenezo, nthawi yomweyo inatumizanso amithenga+ kwa Hezekiya n’kuwauza kuti: 10 “Amuna inu mukamuuze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Usalole Mulungu wako amene ukumudalira kuti akunamize,+ ponena kuti: “Yerusalemu saperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11 Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachita kumayiko onse mwa kuwawononga.+ Ndiye kodi iweyo ukuona ngati upulumuka?+ 12 Kodi milungu+ ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawalanditsa?+ Kodi inalanditsa Gozani,+ Harana,+ Rezefi ndi ana a Edeni+ amene anali ku Tela-sara? 13 Ili kuti mfumu ya Hamati,+ mfumu ya Aripadi,+ ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu,+ Hena, ndi Iva?’”+
14 Kenako Hezekiya anatenga kalatayo m’manja mwa amithengawo n’kuiwerenga.+ Pambuyo pake iye anapita nayo kunyumba ya Yehova, n’kuitambasula pamaso pa Yehova.+ 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera kwa Yehova,+ kuti: 16 “Inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+ 17 Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone, ndipo imvani mawu onse a Senakeribu+ amene watumiza kudzatonza nawo Mulungu wamoyo.+ 18 N’zoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko onse, ndi dziko lawo lomwe.+ 19 Atentha milungu yawo pamoto,+ chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga.+ 20 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ tipulumutseni m’manja mwake,+ kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+
21 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti wapemphera kwa ine za Senakeribu mfumu ya Asuri,+ 22 awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:
“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza ndipo wakuseka.+
Kumbuyo kwako, mwana wamkazi wa Yerusalemu wakupukusira mutu.+
23 Kodi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumulankhula monyoza?+
Ndipo ndani amene iwe wam’kwezera mawu,+
Ndi kum’kwezera maso ako m’mwamba?+
Ndi Woyera wa Isiraeli!+
24 Kudzera mwa antchito ako watonza Yehova ndipo wanena kuti,+
Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+
Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+
Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+
Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+
Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+
25 Ndithu ineyo ndidzakumba zitsime ndi kumwa madzi,
Ndidzaumitsa ndi mapazi anga ngalande zonse zamadzi za mtsinje wa Nailo+ wa ku Iguputo.’+
26 Kodi sunamve?+ Kuyambira nthawi zakale izi n’zimene ndidzachite.+
Ndinakonza zimenezi kuyambira masiku amakedzana.+ Tsopano ndizichita.+
Iweyo udzagwira ntchito yosandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, kukhala yopanda anthu ngati milu ya mabwinja.+
Adzakhala ngati zomera zakutchire, ndi udzu wanthete wobiriwira,+
Ngati udzu womera padenga+ ndiponso wa m’mizere ya m’munda, ukawauka ndi mphepo yotentha yakum’mawa.+
28 Ukakhala phee, ukamatuluka,+ ndiponso ukamalowa, ine ndimadziwa bwino,+
Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+
29 Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga.+
Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+
Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+
30 “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu: Chaka chino mudya mbewu zomera zokha zimene zinagwera pansi.+ Chaka chamawa mudzadya mbewu zongomera zokha, koma chaka chamkuja, anthu inu mudzabzale mbewu n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+ 31 Anthu a m’nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ 32 Chifukwa anthu otsala adzachoka ku Yerusalemu,+ ndipo opulumuka adzachoka kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
33 “‘Chotero Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+ “Sadzalowa mumzinda uno,+ kapena kuponyamo muvi, kapena kufikamo ndi chishango, kapenanso kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo pafupi ndi mpanda wa mzindawu atauzungulira.”’+
34 “‘Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera, ndipo sadzalowa mumzinda uno,’ ndiwo mawu a Yehova.+ 35 ‘Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’”+
36 Ndiyeno mngelo+ wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.+ Anthu podzuka m’mawa, anangoona kuti onse aja ndi mitembo yokhayokha.+ 37 Choncho Senakeribu+ mfumu ya Asuri anachokako n’kubwerera+ kukakhala ku Nineve.+ 38 Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.
38 M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa.+ Choncho mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anabwera kwa iye n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita,+ chifukwa iweyo ufa ndithu. Sukhala ndi moyo.’”+ 2 Atamva mawu amenewa, Hezekiya anatembenukira kukhoma+ n’kuyamba kupemphera kwa Yehova.+ 3 Iye anapemphera kuti: “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.” Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+
4 Tsopano Yehova analankhula+ ndi Yesaya kuti: 5 “Pita, kauze Hezekiya kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako+ wanena kuti: “Ndamva pemphero lako,+ ndipo ndaona misozi yako.+ Tsopano ndiwonjezera zaka 15 pa masiku ako.+ 6 Ndidzalanditsa iweyo ndi mzindawu m’manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzateteza mzinda uno.+ 7 Chizindikiro chochokera kwa Yehova, chakuti Yehova adzakwaniritsadi mawu amene walankhula, ndi ichi:+ 8 Ndichititsa mthunzi wa dzuwa+ umene wapita kale kutsogolo pamasitepe a Ahazi, kuti ubwerere m’mbuyo masitepe 10.”’”+ Choncho dzuwa linabwerera m’mbuyo pang’onopang’ono masitepe 10 pa masitepe pomwe linali litapita kale kutsogolo.+
9 Hezekiya mfumu ya Yuda atadwala+ n’kuchira, analemba zotsatirazi.+
10 Ine ndinati: “Pakatikati pa masiku anga ndidzalowa pazipata+ za Manda.
Ndidzamanidwa zaka zanga zotsala.”+
11 Ndanena kuti: “Sindidzamuona Ya.* Ndithu Ya sindidzam’penya m’dziko la amoyo.+
Anthu sindidzawaonanso. Ndidzakhala ndi anthu okhala kudziko limene kulibe moyo.
12 Malo anga okhala ali ngati hema wa abusa. Mitengo yake yazulidwa ndipo hemayo wachotsedwapo.+
Ndakulunga moyo wanga ngati munthu wowomba nsalu.
Winawake wandidula+ ngati mmene amadulira nsalu kuchowombera nsalu akamaliza kuiwomba.
Kuyambira m’mawa mpaka usiku mumandipereka ku zowawa.+
13 Ndadzitonthoza mpaka m’mawa.+
Mafupa anga onse, iye akungokhalira kuwaphwanya ngati mkango.+
Kuyambira m’mawa mpaka usiku mukungokhalira kundipereka ku zowawa.+
Maso anga akupenyetsetsa kumwamba motopa. Choncho ndinati:+
‘Inu Yehova ine ndapanikizika. Chonde ndithandizeni.’+
15 Kodi ndinene kuti chiyani? Kodi iyeyo andiuza kuti chiyani?+
Iyeyonso wachitapo kanthu.+
Zaka zanga zonse, ndikungokhalira kuyenda ndili khuma chifukwa cha chisoni cha mtima wanga.+
16 ‘Ndi mawu anu, anthu amakhalabe ndi moyo inu Yehova, ndipo mofanana ndi wina aliyense, mzimu wanga umapeza moyo kudzera mu zochita zanu.+
Inu mudzandibwezera thanzi langa n’kundisiya ndi moyo.+
17 M’malo mopeza mtendere ndinapeza zowawa, zowawatu zedi!+
Inuyo mwamamatira moyo wanga ndipo mwauteteza kuti usapite kudzenje la chiwonongeko.+
Pakuti machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.+
18 Pakuti Manda sangakutamandeni.+ Imfa singakulemekezeni.+
Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kukhulupirika kwanu.+
19 Munthu wamoyo, amene akupuma, ndi amene angakutamandeni,+
Ngati mmene ineyo ndikuchitira lero.+
Bambo akhoza kuphunzitsa+ ana ake za kukhulupirika kwanu.
20 Inu Yehova bwerani mudzandipulumutse,+ ndipo tidzaimba nyimbo zimene ine ndinapeka. Ndidzaimba ndi zoimbira za zingwe+
Kunyumba ya Yehova masiku onse a moyo wathu.’”+
21 Kenako Yesaya anati: “Anthu atenge nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndipo azikhukhutize pachithupsa+ chimene ali nacho kuti achire.”+ 22 Pa nthawiyi, Hezekiya anati: “Kodi chizindikiro chakuti ndidzapita kunyumba ya Yehova n’chiyani?”+
39 Pa nthawi imeneyo, Merodaki-baladani+ mwana wa Baladani mfumu ya Babulo,+ anatumiza makalata ndi mphatso+ kwa Hezekiya atamva kuti iye anadwala koma tsopano wapezanso mphamvu.+ 2 Chotero Hezekiya anasangalala ndi alendowo+ ndipo anawaonetsa nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide, mafuta a basamu,+ mafuta abwino, zonse za m’nyumba yake yosungiramo zida zankhondo,+ ndi chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse m’nyumba yake+ ndi mu ufumu wake wonse.+
3 Pambuyo pake, mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya n’kuifunsa kuti:+ “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.”+ 4 Ndiyeno Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani m’nyumba mwanu?”+ Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili m’nyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.” 5 Tsopano Yesaya anauza Hezekiya kuti:+ “Imvani mawu a Yehova wa makamu. 6 ‘Kukubwera masiku amene zinthu zonse zimene zili m’nyumba mwako, ndi zonse zimene makolo ako akhala akusunga kufikira lero, anthu adzazitenga n’kupita nazo ku Babulo.+ Palibe chidzatsale,’+ watero Yehova. 7 ‘Ena mwa ana ako ochokera mwa iwe, amene iweyo udzakhale bambo wawo, nawonso adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna za panyumba+ ya mfumu ya ku Babulo.’”+
8 Pamenepo Hezekiya anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwalankhulawa ndi abwino.”+ Anapitiriza kuti: “Chifukwa bata* ndi mtendere+ zidzapitirira m’masiku anga.”+
40 “Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,” akutero Mulungu wanu anthu inu.+ 2 “Mulankhuleni Yerusalemu momufika pamtima.+ Muuzeni mofuula kuti ntchito yake yogwira mokakamizidwa yatha,+ ndiponso kuti zolakwa zake zalipiridwa.+ Pakuti kuchokera m’dzanja la Yehova, iye walandira malipiro okwanira a machimo ake onse.”+
3 Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti:+ “Konzani njira ya Yehova+ anthu inu! Wongolani msewu wa Mulungu wathu wodutsa m’chipululu.+ 4 Chigwa chilichonse chikwezedwe m’mwamba,+ ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zitsitsidwe.+ Malo okumbikakumbika asalazidwe ndipo malo azitundazitunda akhale chigwa.+ 5 Ulemerero wa Yehova ndithu udzaonekera+ ndipo anthu onse adzauonera limodzi,+ pakuti pakamwa pa Yehova m’pamene panena zimenezi.”+
6 Tamvera! Winawake akunena kuti: “Lankhula mofuula!”+ Ndiye wina akuti: “Ndilankhule mofuula za chiyani?”
“Anthu onse ali ngati udzu wobiriwira ndipo kukoma mtima kwawo konse kosatha kuli ngati maluwa akutchire.+ 7 Udzu wobiriwirawo wauma ndipo maluwawo afota+ chifukwa mpweya wa Yehova wauzirapo.+ Ndithu anthu ali ngati udzu wobiriwira.+ 8 Udzu wobiriwirawo wauma. Maluwawo afota.+ Koma mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”+
9 Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Ziyoni,+ kwera phiri lalitali.+ Lankhula mwamphamvu ndiponso mofuula, iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Yerusalemu.+ Fuula! Usachite mantha.+ Uza mizinda ya ku Yuda kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu.”+ 10 Taonani! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzabwera ngati wamphamvu ndipo dzanja lake lizidzalamulira m’malo mwa iyeyo.+ Mphoto yake ili ndi iyeyo+ ndipo malipiro amene amapereka ali pamaso pake.+ 11 Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa.+ Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake,+ ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.+ Nkhosa zoyamwitsa adzayenda nazo mosamala.+
12 Ndani anayezapo madzi onse a m’nyanja pachikhatho cha dzanja lake?+ Ndani anayezapo kumwamba konse ndi dzanja lake?+ Ndani anayezapo fumbi lonse la padziko lapansi ndi mbale imodzi yokha yoyezera?+ Ndani anayezapo mapiri ndi muyezo, kapena ndani anayezapo zitunda pa sikelo? 13 Ndani anayezapo mzimu wa Yehova? Ndi munthu uti amene angamupatse malangizo kapena kumuphunzitsa kanthu?+ 14 Kodi anafunsirapo nzeru kwa ndani kuti amuthandize kumvetsetsa zinthu? Ndani amamuphunzitsa njira ya chilungamo? Ndani amamuphunzitsa kuti azidziwa zinthu,+ ndipo ndani amamuphunzitsa kuti akhale womvetsa bwino zinthu?+
15 Taonani! Mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko, ndipo kwa iye ili ngati fumbi pasikelo.+ Iyetu amanyamula zilumba+ ngati kuti ndi fumbi. 16 Ngakhale mitengo yonse ya ku Lebanoni singakwane kusonkhezera moto kuti usazime, ndipo nyama zake zam’tchire+ si zokwanira kukhala nsembe yopsereza.+ 17 Mitundu yonse ndi yopanda pake pamaso pake.+ Amaiona ngati si kanthu n’komwe, ngati kuti iyo kulibe.+
18 Kodi anthu inu Mulungu mungamuyerekezere ndi ndani,+ ndipo kodi mungapange chiyani choti mumufanizire nacho?+ 19 Mmisiri wapanga chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Mmisiri wina wa zitsulo wachikuta ndi golide,+ ndipo akuchipangira matcheni asiliva.+ 20 Munthu amasankha mtengo wosawola kuti ukhale ngati chopereka.+ Amafunafuna mmisiri waluso kuti amupangire chifaniziro chosema+ chimene sichingagwedezeke.+
21 Kodi anthu inu simukudziwa? Kodi simunamve? Kodi simunauzidwe kuyambira pa chiyambi? Kodi simunamvetsetse umboni umene wakhalapo kuyambira pamene dziko lapansi linakhalapo?+ 22 Pali Winawake amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lozungulira,+ limene okhalamo ake ali ngati ziwala. Iye anayala kumwamba ngati nsalu yopyapyala, ndipo anakutambasula ngati hema wokhalamo.+ 23 Iye amatsitsa anthu olemekezeka, ndipo amachititsa oweruza a padziko lapansi kuoneka ngati sanakhalepo n’komwe.+
24 Iwo sanabzalidwe n’komwe ndipo sanafesedwe. Chitsa chawo sichinazike mizu munthaka.+ Munthu akhoza kungowauzira iwo n’kuuma,+ ndipo mphepo yamkuntho idzawauluza ngati mapesi.+
25 “Koma kodi anthu inu mungandiyerekezere ndi ndani kuti ndifanane naye?” akutero Woyerayo.+ 26 “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?+ Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi chiwerengero chake, ndipo amaziitana potchula iliyonse dzina lake.+ Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa,+ ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu, palibe imene imasowa.
27 “N’chifukwa chiyani iwe Yakobo, iwe Isiraeli, ukunena kuti: ‘Njira yanga yabisika kwa Yehova,+ ndipo zoti anthu sakundichitira chilungamo Mulungu wanga sakuziona’?+ 28 Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve?+ Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.+ Iye satopa kapena kufooka.+ Palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.+ 29 Iye amapereka mphamvu kwa munthu wotopa,+ ndipo wofooka amam’patsa nyonga zochuluka.+ 30 Anyamata adzatopa n’kufooka ndipo amuna achinyamata adzapunthwa, 31 koma anthu odalira+ Yehova adzapezanso mphamvu.+ Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga.+ Adzathamanga koma osafooka. Adzayenda koma osatopa.”+
41 “Zilumba inu,+ mvetserani mawu anga mutakhala chete, ndipo mitundu ya anthu+ ipezenso mphamvu. Ibwere pafupi,+ kenako ilankhule. Anthu inu bwerani kufupi nane kumalo oweruzira mlandu.+
2 “Kodi ndani anautsa winawake kuchokera kotulukira dzuwa?+ Kodi ndani anamuitana mwachilungamo kuti ayandikire kumapazi ake, kuti amupatse mitundu ya anthu pamaso pake, ndiponso kuti amuchititse kupita kukagonjetsa ngakhale mafumu?+ Kodi ndani amene anali kuwapereka kulupanga lake ngati fumbi, moti auluzika ndi uta wake ngati mapesi?+ 3 Kodi ndani amene anali kuwathamangitsa? Ndani amene anali kuyenda mwamtendere ndi mapazi ake panjira imene anali asanadutsepo n’komwe? 4 Ndani wachita zimenezi,+ kuitana mibadwo kuyambira pa chiyambi?+
“Ndineyo Yehova, Woyamba,+ ndipo ndidzakhala chimodzimodzi ngakhale kwa omalizira.”+
5 Zilumba+ zinaona n’kuyamba kuopa. Malekezero a dziko lapansi anayamba kunjenjemera.+ Mitundu ya anthu inasonkhana pamodzi n’kumangobwerabe. 6 Aliyense anali kuthandiza mnzake, ndipo munthu anali kuuza mbale wake kuti: “Limba mtima.”+ 7 Chotero mmisiri wa mitengo anali kulimbikitsa mmisiri wa zitsulo.+ Amene anali kusalaza zitsulo ndi nyundo anali kulimbikitsa amene anali kumenya zitsulo ndi nyundo. Ponena za ntchito yowotcherera zitsulo ndi mtovu, iye anati: “Zili bwino.” Pomalizira pake, wina anakhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwedezeke.+
8 “Koma iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga,+ iwe Yakobo amene ndakusankha,+ mbewu ya bwenzi langa+ Abulahamu.+ 9 Ndakutenga kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+ ndiponso ndakuitana kuchokera kumadera akutali a dziko lapansi.+ Chotero ndinakuuza kuti, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga.+ Ndasankha iweyo+ ndipo sindinakutaye.+ 10 Usachite mantha, pakuti ndili nawe.+ Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.+ Ndikulimbitsa.+ Ndithu ndikuthandiza.+ Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja+ lachilungamo.’+
11 “Taona! Onse okupsera mtima adzachita manyazi ndipo adzanyozeka.+ Anthu amene akukangana nawe sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.+ 12 Anthu amene akulimbana nawe udzawafunafuna koma sudzawapeza. Anthu amene akumenyana nawe+ adzakhala ngati kulibeko ndipo sadzakhalanso ngati kanthu.+ 13 Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja.+ Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha.+ Ineyo ndikuthandiza.’+
14 “Usachite mantha, nyongolotsi iwe+ Yakobo, inuyo amuna a Isiraeli.+ Ineyo ndikuthandizani,” akutero Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli. 15 “Taona! Ndakusandutsa chopunthira mbewu,+ chida chatsopano chopunthira mbewu chokhala ndi mano. Udzapondaponda mapiri n’kuwaphwanya, ndipo zitunda udzazisandutsa mankhusu.+ 16 Udzapeta+ mapiri ndi zitundazo ndipo mphepo idzaziuluza.+ Mphepo yamkuntho idzaziuluzira kumalo osiyanasiyana.+ Iweyo udzasangalala chifukwa cha Yehova.+ Udzadzitama chifukwa cha Woyera wa Isiraeli.”+
17 “Anthu ozunzika ndi osauka akufunafuna madzi,+ koma sakuwapeza. Lilime lawo lauma ndi ludzu.+ Ineyo Yehova ndidzawayankha.+ Ineyo Mulungu wa Isiraeli, sindidzawasiya.+ 18 Ndidzatsegula mitsinje pamapiri opanda zomera zilizonse, ndipo pakatikati pa zigwa ndidzatsegulapo akasupe.+ Chipululu ndidzachisandutsa dambo lamadzi, ndipo dziko lopanda madzi ndidzalisandutsa pochokera madzi.+ 19 M’chipululu ndidzabzalamo mtengo wa mkungudza, mtengo wa mthethe, mtengo wa mchisu, ndi mtengo wamafuta.+ M’dera lachipululu ndidzabzalamo mtengo wofanana ndi mkungudza, mtengo wa ashi,* ndi mtengo wa paini pa nthawi imodzimodziyo.+ 20 Ndidzachita zimenezi kuti anthu onse pamodzi aone, adziwe, amve, ndiponso azindikire, kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi, ndiponso kuti Woyera wa Isiraeli ndi amene wachititsa zimenezi.”+
21 “Bweretsani kuno mlandu wanu wovuta,”+ akutero Yehova. “Nenani mfundo zanu,”+ ikutero Mfumu ya Yakobo.+ 22 “Tionetseni ndipo mutiuze zinthu zimene zidzachitike. Tiuzeni kuti zinthu zoyambirira zinali zotani, kuti tiziganizire mozama mumtima mwathu ndi kudziwa tsogolo lake. Kapena mutiuze zinthu zimene zikubwera.+ 23 Nenani zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, kuti tidziwe kuti inu ndinu milungu.+ Inde, muyenera kuchita zabwino kapena zoipa, kuti tizionere limodzi ndi kuchita mantha.+ 24 Taonani! Inuyo sindinu kanthu ndipo zimene mwachita si kanthu.+ Aliyense wokusankhani ndi wochititsa nyansi.+
25 “Ine ndautsa winawake kuchokera kumpoto, ndipo abwera.+ Iye adzaitana pa dzina langa kuchokera kotulukira dzuwa.+ Adzaukira atsogoleri ngati kuti ndi dongo+ ndiponso ngati kuti iyeyo ndi woumba amene amapondaponda dongo laliwisi.
26 “Kodi ndani wanenapo chilichonse kuchokera pa chiyambi kuti tidziwe, kapena kuchokera nthawi zakalekale kuti tinene kuti, ‘Akunena zoona’?+ Ndithu palibe amene akunena chilichonse. Ndithu palibe amene akulankhula chilichonse kuti anthu amve. Ndithu palibe aliyense amene akumva mawu alionse a anthu inu.”+
27 Pali woyamba, amene akunena kwa Ziyoni kuti: “Tamverani zimene zidzachitike!”+ Yerusalemu ndidzamupatsa munthu wobweretsa uthenga wabwino.+
28 Ndinapitiriza kuyang’ana, koma panalibe munthu aliyense. Pakati pa mafanowo panalibe aliyense amene anali kupereka malangizo,+ ndipo ndinapitiriza kuwafunsa kuti ayankhe. 29 Onsewo ali ngati chinthu choti kulibeko. Ntchito zawo si kanthu. Mafano awo opangidwa ndi zitsulo zosungunula ali ngati mphepo ndiponso zinthu zomwe si zenizeni.+
42 Taonani mtumiki wanga+ amene ndamugwiritsitsa,+ amene ndamusankha,+ ndiponso amene moyo wanga ukukondwera naye.+ Ine ndaika mzimu wanga mwa iye,+ ndipo iye adzabweretsa chilungamo kwa anthu a mitundu ina.+ 2 Iye sadzafuula kapena kukweza mawu ake, ndipo mawu ake sadzamvedwa mumsewu.+ 3 Bango lophwanyika sadzalithyola,+ ndipo chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima sadzachizimitsa. Iyeyo adzabweretsa chilungamo mokhulupirika.+ 4 Iye sadzatsala pang’ono kuzima kapena kuphwanyidwa mpaka atakhazikitsa chilungamo padziko lapansi.+ Zilumba zidzadikirira lamulo lake.+
5 Mulungu woona Yehova, amene analenga kumwamba+ ndiponso Wokutambasula Wamkulu,+ amene anakhazikitsa dziko lapansi+ ndi zonse zimene zili mmenemo,+ amene anapereka mpweya+ kwa anthu amene ali mmenemo,+ ndi mzimu kwa anthu amene amayenda padzikopo,+ iye wanena kuti: 6 “Ineyo Yehova pochita zinthu mwachilungamo, ndinakuitana+ ndipo ndinakugwira dzanja.+ Ndidzakuteteza ndiponso ndidzakupereka monga pangano kwa anthu+ ngati kuwala kwa mitundu ya anthu,+ 7 kuti ukatsegule maso a akhungu,+ ukatulutse mkaidi m’ndende ya mdima+ ndiponso kuti ukatulutse m’ndende anthu amene ali mu mdima.+
8 “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli,+ ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense+ kapena kupereka ulemerero wanga+ kwa zifaniziro zogoba.+
9 “Zinthu zoyamba zachitika,+ koma ndikukuuzani zinthu zatsopano. Zisanayambe kuonekera, ndimakuuzani.”+
10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+ M’tamandeni kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ M’tamandeni inu amuna amene mumadalira nyanja+ ndi zonse zokhala mmenemo, ndiponso inu zilumba ndi anthu okhala m’zilumbazo.+ 11 Chipululu+ ndi mizinda ya kumeneko, ndiponso midzi ya ku Kedara zikweze mawu awo.+ Anthu okhala m’dera lamatanthwe+ afuule mokondwera. Anthu afuule kuchokera pamwamba pa mapiri. 12 Anthu am’patse Yehova ulemerero,+ ndipo anthu a m’zilumba anene za ulemerero wake.+
13 Yehova adzanyamuka ngati munthu wamphamvu.+ Ngati wankhondo, iye adzachita zinthu modzipereka kwambiri.+ Iye adzafuula, ndithu adzafuula mfuu yankhondo,+ ndipo adzakhala wamphamvu kuposa adani ake.+
14 “Ndakhala phee kwa nthawi yaitali.+ Ndinangokhala chete.+ Ndakhala ndikudziletsa.+ Tsopano ndibuula, ndipuma movutikira, ndipo ndipuma mwawefuwefu pa nthawi imodzimodziyo, ngati mkazi amene akubereka.+ 15 Ndidzawononga+ mapiri ndi zitunda. Ndidzaumitsa zinthu zonse zimene zinamera mmenemo. Mitsinje ndidzaisandutsa zilumba ndipo madambo ndidzawaumitsa.+ 16 Anthu akhungu ndidzawayendetsa m’njira imene sakuidziwa.+ Ndidzawadutsitsa mumsewu umene sakuudziwa.+ Malo amdima ndidzawasandutsa kuwala pamaso pawo,+ ndipo malo okumbikakumbika ndidzawasalaza.+ Zimenezi ndi zimene ndidzawachitire ndipo sindidzawasiya.”+
17 Anthu amene akudalira zifaniziro zosema, amene akuuza zifaniziro zopangidwa ndi chitsulo chosungunula kuti: “Ndinu milungu yathu,” adzathawa ndipo adzachita manyazi kwambiri.+
18 Inu ogontha imvani. Inu akhungu yang’anani kuti muone.+ 19 Ndani amene ali wakhungu? Mtumiki wanga ndiye wakhungu. Ndani amene ali wogontha ngati mtumiki wanga amene ndamutuma? Ndani amene ali wakhungu ngati munthu amene wapatsidwa mphoto, kapena amene ali wakhungu ngati mtumiki wa Yehova?+ 20 Iwe waona zinthu zambiri, koma sunachitepo kanthu.+ Makutu ako akhala ali otseguka koma sunamvetsere.+ 21 Chifukwa cha chilungamo chake,+ Yehova walemekeza ndi kukweza malamulo ake mokondwera.+ 22 Koma anthu amenewa agwidwa ndipo atengedwa.+ Onsewa anagwera m’maenje ndipo akhala akubisidwa m’ndende.+ Atengedwa popanda wowalanditsa.+ Agwidwa popanda wonena kuti: “Bwererani nawo!”
23 Ndani pakati panu amene adzamvetsere zinthu zimenezi? Ndani adzatchere khutu ndi kumvetsera zinthu zimene zidzamuthandize m’tsogolo?+ 24 Ndani wachititsa kuti Yakobo angokhala zofunkha ndiponso kupereka Isiraeli kwa anthu olanda? Kodi si Yehova amene iwo am’chimwira, amene sanafune kuyenda m’njira zake ndipo sanasunge malamulo ake?+ 25 Choncho Mulungu anali kuwakhuthulira mkwiyo, ukali wake, ndi nkhondo yoopsa.+ Nkhondoyo inali kuwapsereza+ koma iwo sanazindikire.+ Inapitiriza kuwatentha koma iwo sanaganizire chilichonse mumtima mwawo.+
43 Tsopano iwe Yakobo, mvera zimene wanena Yehova Mlengi wako,+ yemwe anakupanga+ iwe Isiraeli. Iye wanena kuti: “Usachite mantha, pakuti ine ndakuwombola.+ Ndakuitana pokutchula dzina.+ Iwe ndiwe wanga.+ 2 Ukamadzadutsa pamadzi,+ ine ndidzakhala nawe.+ Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakumiza.+ Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.+ 3 Pakuti ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Isiraeli ndiponso Mpulumutsi wako.+ Ndapereka Iguputo monga dipo* lokuwombolera.+ Ndaperekanso Itiyopiya+ ndi Seba m’malo mwako. 4 Chifukwa chakuti ndiwe wamtengo wapatali kwa ine,+ ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.+ Ndidzapereka anthu m’malo mwa iwe, ndipo ndidzapereka mitundu ya anthu m’malo mwa moyo wako.+
5 “Usachite mantha chifukwa ine ndili nawe.+ Ndidzabweretsa mbewu yako kuchokera kotulukira dzuwa, ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kolowera dzuwa.+ 6 Ndidzauza kumpoto kuti,+ ‘Abwezere kwawo!’ ndipo ndidzauza kum’mwera kuti, ‘Usawakanize! Bweretsa ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ 7 Bweretsa aliyense amene amatchedwa ndi dzina langa,+ amene ndinamulenga chifukwa cha ulemerero wanga,+ amene ndinamuumba ndiponso amene ndinamupanga.’+
8 “Bweretsa anthu akhungu ngakhale kuti ali ndi maso, ndiponso anthu ogontha ngakhale kuti ali ndi makutu.+ 9 Mitundu yonse isonkhanitsidwe pamalo amodzi, ndipo mitundu ya anthu ikhale pamodzi.+ Ndani pakati pawo amene anganene zimenezi?+ Kapena ndani amene angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+ Abweretse mboni zawo+ kuti akhale olungama ndipo mbonizo zimve ndi kunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+
10 “Inu ndinu mboni zanga,”+ akutero Yehova. “Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani+ kuti mundidziwe+ ndi kundikhulupirira,+ komanso kuti mumvetse kuti ine sindinasinthe.+ Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa,+ ndipo pambuyo panga palibenso wina.+ 11 Ine ndine Yehova.+ Popanda ine palibenso mpulumutsi wina.”+
12 “Ine ndanena ndipo ndapulumutsa.+ Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo,+ ine ndinachititsa kuti chipulumutsocho chimveke. Choncho inuyo ndinu mboni zanga,+ ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.+ 13 “Komanso, nthawi zonse ine sindisintha.+ Palibenso wina amene angathe kupulumutsa anthu m’dzanja langa.+ Ndikayamba kuchitapo kanthu,+ ndani amene angalimbane ndi dzanja langa?”+
14 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Chifukwa cha inu, ndidzawatumiza ku Babulo. Ndidzachititsa kuti zitsulo za ndende zimasuke+ ndiponso ndidzagonjetsa Akasidi amene ali m’zombo ndi kuwachititsa kulira mokuwa.+ 15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu,+ Mlengi wa Isiraeli+ ndiponso Mfumu yanu.”+
16 Izi n’zimene Yehova wanena, yemwe amapanga njira panyanja. Amapanga msewu ngakhale pamadzi amphamvu.+ 17 Amatsogolera magaleta ankhondo ndi mahatchi, komanso gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu pa nthawi imodzi.+ Iye wanena kuti: “Iwo adzagona pansi,+ sadzadzuka+ ndipo adzatha.+ Adzazimitsidwa ngati chingwe cha nyale.”+
18 “Musakumbukire zinthu zoyambirira, ndipo musaganizirenso zinthu zakale. 19 Taonani! Ndikupanga zinthu zatsopano.+ Zimenezi zionekera ndipo anthu inu muzidziwa ndithu.+ M’chipululu, ine ndidzatsegulamo njira+ ndi mitsinje.+ 20 Zilombo zakutchire zidzanditamanda.+ Mimbulu ndi nthiwatiwa+ zidzanditamanda chifukwa ndidzapereka madzi ndi mitsinje m’chipululu,+ kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe, 21 ndiponso kuti anthu amene ndinawapanga kuti akhale anga, anene za ulemerero wanga.+
22 “Koma iwe Yakobo, iwe Isiraeli, sunapemphe thandizo kwa ine+ chifukwa chakuti watopa nane.+ 23 Iwe sunandibweretsere nkhosa zako zansembe zopsereza zathunthu. Sunandilemekeze ndi nsembe zako.+ Ine sindinakuumirize kuti uzindipatsa mphatso ndipo sindinakutopetse n’kukupempha lubani.*+ 24 Iwe sunandigulire bango lonunkhira+ ndi ndalama iliyonse, ndipo sunandikhutitse ndi mafuta a nsembe zako.+ Koma m’malomwake, wandiumiriza ndi machimo ako kuti ndikutumikire. Wanditopetsa ndi zolakwa zako.+
25 “Ineyo ndi amene ndikufafaniza+ zolakwa zako,+ ndipo machimo ako sindidzawakumbukiranso.+ 26 Tiye tikhale pa mlandu. Ndikumbutse.+ Fotokoza mbali yako kuti iweyo ukhale wosalakwa.+ 27 Bambo wako, woyamba uja, anachimwa+ ndipo anthu okulankhulira andilakwira.+ 28 Chotero ndidzadetsa akalonga a pamalo oyera. Yakobo ndidzamuwononga ndipo Isiraeli ndidzamunyozetsa.+
44 “Tsopano mvetsera, iwe Yakobo mtumiki wanga,+ ndi iwe Isiraeli amene ndakusankha.+ 2 Yehova, amene anakupanga+ ndiponso amene anakuumba,+ amene anali kukuthandiza ngakhale pamene unali m’mimba,+ wanena kuti, ‘Usachite mantha,+ iwe mtumiki wanga Yakobo, ndiponso iwe Yesuruni,+ amene ndakusankha. 3 Pakuti ndidzapatsa madzi munthu waludzu,+ ndipo ndidzaika timitsinje tamadzi pamalo ouma.+ Ndidzatsanulira mzimu wanga pambewu yako+ ndi madalitso anga pa mbadwa zako. 4 Iwo adzaphuka ngati udzu wobiriwira,+ ndiponso ngati mitengo ya msondodzi+ m’mphepete mwa ngalande zamadzi. 5 Uyu adzati: “Ine ndine wa Yehova.”+ Uyo adzadzitcha dzina la Yakobo,+ ndipo wina adzalemba padzanja lake kuti: “Wa Yehova.” Munthu winanso adzadzipatsa dzina la Isiraeli.’+
6 “Yehova, Mfumu ya Isiraeli,+ Womuwombola iye,+ Yehova wa makamu, wanena kuti: ‘Ine ndine woyamba ndi womaliza,+ ndipo palibenso Mulungu kupatulapo ine.+ 7 Ndani ali ngati ine?+ Ayankhe molimba mtima kuti apereke umboni wake kwa ine.+ Monga momwe ine ndachitira kuyambira nthawi imene ndinakhazikitsa anthu akalekale,+ iwo anene zinthu zimene zichitike posachedwa ndi zimene zidzachitike m’tsogolo. 8 Anthu inu musachite mantha ndipo musathedwe nzeru.+ Kodi sindinachititse aliyense wa inu kuti amve kuyambira nthawi imeneyo? Kodi sindinakuuzeni zimenezi?+ Inu ndinu mboni zanga.+ Kodi palinso Mulungu kupatulapo ine?+ Ayi, palibe Thanthwe.+ Sindikudziwapo aliyense.’”
9 Anthu onse opanga zifaniziro zosema ndi opanda pake,+ ndipo mafano awo okondedwa adzakhala opanda phindu.+ Monga mboni zawo, mafanowo saona chilichonse ndipo sadziwa chilichonse,+ kuti anthu opanga mafanowo achite manyazi.+ 10 Kwa aliyense amene wapanga mulungu kapena kuumba fano lopangidwa ndi chitsulo chosungunula,+ lidzakhala lopanda phindu ngakhale pang’ono.+ 11 Anzake onse adzachita manyazi,+ ndipotu amisiriwo ndi anthu ochokera kufumbi. Onsewo adzasonkhana pamodzi.+ Adzaima chilili. Adzachita mantha. Onsewo adzachitira limodzi manyazi.+
12 Munthu wogoba zitsulo ndi chogobera watentha chitsulocho ndi makala amoto. Wachiwongola ndi nyundo, ndipo wakhala ali jijirijijiri kuchiumba ndi dzanja lake lamphamvu.+ Wamva njala ndipo alibe mphamvu. Sanamwe madzi, chotero watopa.
13 Mmisiri wosema mtengo watambasula chingwe choyezera. Waulemba ndi choko chofiira. Wausema ndi sompho ndipo waulemberera ndi chida cholembera mizere yozungulira. Pang’ono ndi pang’ono waupanga kuti uzioneka ngati munthu,+ ngati kukongola kwa anthu, kuti uzikhala m’nyumba.+
14 Pali munthu amene ntchito yake ndi yogwetsa mitengo ya mkungudza. Iye amasankha mtengo wamtundu winawake, waukulu kwambiri, n’kuusiya kuti ukule n’kukhwima pakati pa mitengo ya m’nkhalango.+ Iye anabzala mtengo wa paini, ndipo mvula yaukulitsa kwambiri. 15 Tsopano mtengowo wafika poti munthu akhoza kuusandutsa nkhuni. Chotero iye watenga mbali ya mtengowo kuti asonkhere moto woti aziwotha. Wayatsa motowo n’kuphikapo mkate. Wasemanso mulungu woti azimugwadira.+ Mtengowo waupanga chifaniziro chosema+ ndipo akuchigwadira n’kumachilambira. 16 Hafu ya mtengowo waitentha pamoto. Hafu ina ya mtengowo wawotchera nyama imene wadya, ndipo wakhuta. Wawothanso moto wake ndipo wanena kuti: “Eya! Ndafundidwa. Ndaona kuwala kwa moto.” 17 Koma mtengo wotsalawo wapangira mulungu, wapangira chifaniziro chake chosema. Wachiweramira ndi kuchigwadira n’kumapemphera pamaso pake kuti: “Ndipulumutseni, pakuti ndinu mulungu wanga.”+
18 Iwo sadziwa chilichonse+ ndipo samvetsetsa chilichonse+ chifukwa maso awo amatidwa kuti asamaone,+ ndipo mitima yawo ndi yosazindikira zinthu.+ 19 Palibe amene akuganiza mumtima mwake+ kapena amene akudziwa zinthu, kapenanso amene ali womvetsa zinthu+ kuti adzifunse kuti: “Hafu ya mtengowu ndasonkhera moto ndipo pamakala ake ndaphikapo mkate. Ndawotchanso nyama n’kudya. Koma kodi wotsalawu ndipangire chinthu chonyansa?+ Kodi zoona ndiweramire mtengo woumawu?” 20 Iye akudya phulusa.+ Mtima wake umene wanyengedwa wamusocheretsa.+ Iye sakupulumutsa moyo wake kapena kunena kuti: “Kodi chinthu chimene chili m’dzanja langa lamanjachi si chonyenga?”+
21 “Kumbukira zinthu zimenezi iwe Yakobo,+ ndiponso iwe Isiraeli, pakuti ndiwe mtumiki wanga.+ Ine ndiye amene ndinakuumba.+ Iweyo ndiwe mtumiki wanga. Iwe Isiraeli, ine sindikuiwala.+ 22 Ndidzafafaniza zolakwa zako ngati kuti ndaziphimba ndi mtambo,+ ndi machimo ako ngati kuti ndawaphimba ndi mitambo yambiri. Bwerera kwa ine,+ ndipo ine ndikuwombola.+
23 “Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ pakuti Yehova wachitapo kanthu.+ Fuulani mosangalala,+ inu malo otsika kwambiri a dziko lapansi.+ Mapiri+ inu ndiponso iwe nkhalango ndi inu mitengo yonse ili mmenemo, kondwani ndi kufuula ndi chisangalalo. Pakuti Yehova wawombola Yakobo ndipo wasonyeza kukongola kwake pa Isiraeli.”+
24 Yehova, Wokuwombola+ ndiponso amene anakuumba kuyambira uli m’mimba, wanena kuti: “Ine Yehova ndachita zonse. Ndinatambasula ndekha kumwamba,+ ndi kukhazikitsa dziko lapansi.+ Kodi ndani anali nane? 25 Ndimalepheretsa zizindikiro za anthu olankhula zinthu zopanda pake, ndipo ndine amene ndimachititsa olosera kuchita zamisala.+ Ndine amene ndimachititsa anthu anzeru kubwerera kumbuyo, ndiponso amene ndimachititsa nzeru zawo kukhala zopusa.+ 26 Ndine amene ndimachititsa mawu a mtumiki wanga kukwaniritsidwa ndiponso amene ndimakwaniritsa mawu onse amene atumiki anga analengeza.+ Ndine amene ndikunena za Yerusalemu kuti, ‘Muzidzakhala anthu.’+ Ndikunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti, ‘Idzamangidwanso,+ ndipo malo ake osakazidwa ndidzawamanganso.’+ 27 Ndine amene ndikuuza madzi akuya kuti, ‘Iphwa ndipo mitsinje yako yonse ndidzaiumitsa.’+ 28 Ndine amene ndikunena za Koresi+ kuti, ‘Iye ndi m’busa wanga ndipo adzakwaniritsa bwinobwino zonse zimene ndikufuna,’+ ngakhale zimene ndanena zokhudza Yerusalemu zakuti, ‘Adzamangidwanso,’ ndi zokhudza kachisi zakuti, ‘Maziko ako adzamangidwa.’”+
45 Ine Yehova ndalankhula kwa wodzozedwa wanga.+ Ndalankhula kwa Koresi amene ndamugwira dzanja lake lamanja+ kuti ndigonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+ kuti ndimasule m’chiuno mwa mafumu, kuti ndimutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri, moti ngakhale zipata sizidzatsekedwa. Ndalankhula kuti: 2 “Ine ndidzakhala kutsogolo kwako+ ndipo ndidzasalaza zitunda za m’dzikolo.+ Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuwa ndipo ndidzadula mipiringidzo yachitsulo.+ 3 Ndidzakupatsa chuma+ chimene chili mu mdima ndi chuma chobisika chimene chili m’malo achinsinsi, kuti udziwe kuti ine ndine Yehova, Mulungu wa Isiraeli, amene ndikukuitana ndi dzina lako.+ 4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo ndi Isiraeli wosankhidwa wanga,+ ine ndinakuitana ndi dzina lako. Ndinakupatsa dzina laulemu, ngakhale kuti sunali kundidziwa.+ 5 Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.+ Palibenso Mulungu kupatulapo ine.+ Ndidzakumanga mwamphamvu m’chiuno mwako, ngakhale kuti sukundidziwa, 6 kuti anthu adziwe kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kolowera dzuwa kuti palibenso wina kupatulapo ine.+ Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+ 7 Ndimapanga kuwala+ ndiponso ndimabweretsa mdima.+ Ndimabweretsa mtendere+ ndiponso tsoka.+ Ine Yehova ndimapanga zonsezi.+
8 “Inu kumwamba, chititsani chilungamo kuvumba ngati mvula.+ Kumwamba kwa mitambo kuchuche chilungamo.+ Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso. Lichititse chilungamo kuphuka+ pa nthawi imodzimodziyo. Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”+
9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”? 10 Tsoka kwa wofunsa bambo kuti: “Kodi n’chiyani mwaberekachi?” Ndiponso wofunsa mkazi kuti: “Kodi zowawa za pobereka zimene mukumvazi mukufuna mubereke chiyani?”+
11 Yehova, Woyera wa Isiraeli+ ndiponso amene anamuumba,+ wanena kuti: “Ndifunseni za zinthu zimene zikubwera+ zokhudza ana anga.+ Ndipo pa zinthu zokhudza ntchito+ ya manja anga mundifunse kuti ndikuyankheni. 12 Ineyo ndinapanga dziko lapansi+ ndipo ndinalenga munthu n’kumuikapo.+ Manja anga anatambasula kumwamba,+ ndipo nyenyezi ndi zonse zimene zili kumwambako ndimazilamulira.”+
13 “Ine ndautsa winawake m’chilungamo+ ndipo njira zake zonse ndidzaziwongola.+ Iye ndi amene adzamange mzinda wanga+ ndipo anthu anga amene ali ku ukapolo adzawamasula,+ koma osati ndi malipiro+ kapena ndi chiphuphu,” watero Yehova wa makamu.
14 Yehova wanena kuti: “Antchito osalipidwa a ku Iguputo,+ amalonda a ku Itiyopiya, ndi Asabeya,+ amuna ataliatali,+ adzabwera kwa iwe ndipo adzakhala ako.+ Iwo adzayenda pambuyo pako. Adzabwera kwa iwe atamangidwa m’matangadza+ ndipo adzakugwadira.+ Adzapemphera kwa iwe kuti, ‘Zoonadi Mulungu ali ndi iwe+ ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu wina.’”+
15 Ndithu, inu ndinu Mulungu yemwe amadzibisa,+ Mulungu wa Isiraeli, Mpulumutsi.+ 16 Anthu adzachita manyazi ndipo onsewo adzanyozeka. Anthu opanga mafano adzayenda monyozeka onse pamodzi.+ 17 Koma Isiraeli adzapulumutsidwa chifukwa chokhala pa mgwirizano ndi Yehova+ ndipo adzakhala wopulumutsidwa mpaka kalekale.+ Anthu inu simudzachita manyazi+ ndipo simudzanyozeka+ mpaka kalekale, ngakhale kwamuyaya.
18 Pakuti Yehova, Mlengi wa kumwamba,+ Mulungu woona,+ amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga,+ amene analikhazikitsa mwamphamvu,+ amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti: “Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+ 19 Ine sindinalankhule m’malo obisika,+ m’malo amdima a padziko lapansi. Sindinauze mbewu ya Yakobo kuti, ‘Anthu inu muzindifunafuna pachabe.’+ Ine ndine Yehova, wolankhula zolungama, wonena zowongoka.+
20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+ 21 Lankhulani ndipo mufotokoze mlandu wanu.+ Inde, iwo afunsanefunsane mogwirizana. Kodi ndani wachititsa zimenezi kuti zimveke kuyambira kalekale?+ Ndani wazinena kuyambira nthawi imene ija?+ Kodi si ine Yehova, amene palibenso Mulungu wina kupatulapo ine?+ Ine ndine Mulungu wolungama ndi Mpulumutsi+ ndipo palibenso wina kupatulapo ine.+
22 “Tembenukirani kwa ine kuti mupulumuke,+ inu nonse amene muli kumapeto kwa dziko lapansi, pakuti ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.+ 23 Ndalumbira pa ine mwini.+ Mawuwo atuluka m’kamwa mwanga m’chilungamo,+ moti sadzabwerera.+ Ndalumbira kuti bondo lililonse lidzagwadira ine+ ndipo lilime lililonse lidzalumbira kwa ine,+ 24 kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chonse ndi mphamvu.+ Onse omukwiyira adzabwereranso kwa iyeyo n’kuchita manyazi.+ 25 Mbewu+ yonse ya Isiraeli idzaona kuti inalondola+ potumikira Yehova ndipo idzadzitama.’”+
46 Beli+ wawerama+ ndipo Nebo wagwada. Mafano awo+ akhala katundu wa nyama zakutchire ndi wa nyama zoweta. Mafanowo angokhala katundu wolemera kwa nyama zotopa. 2 Milungu imeneyi idzawerama, ndipo yonse pamodzi idzagwada pansi. Singapulumutse zifaniziro zawo+ zimene zanyamulidwa ngati katundu, koma idzatengedwa kupita ku ukapolo.+
3 “Inu a nyumba ya Yakobo ndimvetsereni. Ndimvetsereni inu nonse otsala a m’nyumba ya Isiraeli,+ inu amene ndinakunyamulani kuyambira pamene munabadwa, ndiponso inu amene ndinakusamalirani kuyambira pamene munatuluka m’mimba.+ 4 Ine sindisintha ngakhale kwa wokalamba,+ ndipo munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.+ Ndithu ineyo ndidzachitapo kanthu+ kuti ndiwatenge, ndiwanyamule ndi kuwapulumutsa.+
5 “Kodi anthu inu mungandifanizire ndi ndani,+ kapena mungandiyerekezere ndi ndani?+ 6 Pali anthu amene amakhuthula golide m’zikwama, ndi kuyeza siliva pasikelo. Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo iye amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+ Kenako anthuwo amayamba kuweramira ndi kugwadira mulunguyo.+ 7 Iwo amamunyamula pamapewa awo.+ Amamutenga n’kukamuika pamalo ake ndi kumuimika bwinobwino. Mulunguyo sayenda kuchoka pamalo akewo.+ Ngakhale munthu atamufuulira, iye sayankha. Sapulumutsa munthu kumavuto ake.+
8 “Anthu inu kumbukirani izi kuti mulimbe mtima. Muziganizire mumtima mwanu,+ inu anthu ochimwa.+ 9 Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,+ kuti ine ndine Mulungu+ ndipo palibenso Mulungu wina,+ kapena aliyense wofanana ndi ine.+ 10 Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.+ Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.+ Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi,+ ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+ 11 Ine ndi amene ndidzaitane mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa.+ Ndidzaitana munthu kuti adzachite zolingalira zanga kuchokera kutali.+ Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita.+ Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.+
12 “Tamverani inu anthu osamva,+ inu anthu amene muli kutali ndi chilungamo.+ 13 Ine ndabweretsa pafupi chilungamo changa.+ Chilungamocho sichili kutali,+ ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa.+ Ndidzapereka chipulumutso mu Ziyoni, ndipo Isiraeli ndidzam’patsa kukongola kwanga.”+
47 Tsika ukhale pansi pafumbi+ iwe namwali, mwana wamkazi wa Babulo.+ Khala padothi pomwe palibe mpando wachifumu,+ iwe mwana wamkazi wa Akasidi.+ Pakuti anthu adzaleka kukutchula kuti ndiwe wolekereredwa ndiponso wosasatitsidwa.*+ 2 Tenga mphero+ upere ufa. Vula nsalu yako yophimba kumutu.+ Vula chovala chako chokhwekhwerera pansi.+ Ukweze chovala chako m’mwamba mpaka miyendo ionekere,+ ndipo uwoloke mitsinje. 3 Vula ukhale maliseche,+ komanso manyazi ako aonekere.+ Ine ndidzabwezera+ ndipo sindidzalekerera aliyense wofuna kunditsekereza.
4 “Pali amene akutiwombola.+ Dzina lake ndi Yehova wa makamu,+ Woyera wa Isiraeli.”+
5 Iwe mwana wamkazi wa Akasidi,+ khala pansi mwakachetechete+ ndipo ulowe mu mdima.+ Pakuti anthu sadzakutchulanso kuti Dona+ wa Maufumu.+ 6 Ine ndinakwiyira anthu anga.+ Ndinanyoza cholowa changa+ ndipo ndinawapereka m’manja mwako.+ Iwe sunawachitire chifundo.+ Munthu wokalamba unamusenzetsa goli lolemera kwambiri.+ 7 Iwe unali kunena kuti: “Ine ndidzakhala Dona mpaka kalekale,+ mpaka muyaya.” Sunaganizire zinthu izi mumtima mwako ndipo sunaganizire kuti zidzatha bwanji.+
8 Tsopano imva izi iwe mkazi wokonda zosangalatsa, wokhala pabwino,+ iwe amene umanena mumtima mwako kuti: “Ndine ndekha, palibenso wina.+ Sindidzakhala wamasiye ndipo ana anga sadzafa.”+ 9 Koma zinthu ziwiri izi zidzakugwera modzidzimutsa tsiku limodzi:+ Ana ako adzafa ndiponso udzakhala wamasiye. Zimenezi zidzakugwera ndithu,+ chifukwa cha zamatsenga zochuluka zimene wachita, chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zako zamatsenga, ndiponso chifukwa chakuti wazichita kwambiri.+ 10 Iwe unali kudalira zoipa zako.+ Wanena kuti: “Palibe amene akundiona.”+ Wasochera chifukwa cha nzeru zako ndiponso chifukwa chodziwa zinthu.+ Mumtima mwako umakhalira kunena kuti: “Ndine ndekha, palibenso wina.” 11 Koma tsoka lidzakugwera ndipo sudzatha kuliletsa ndi matsenga ako. Mavuto adzakugwera+ ndipo sudzatha kuwapewa. Chiwonongeko chimene sunali kuchiyembekezera chidzakupeza modzidzimutsa.+
12 Tsopano imirira, tenga nyanga zako ndiponso zamatsenga zako zambirimbiri+ zomwe wazivutikira kuyambira uli mwana. Uzitenge kuti mwina zingakuthandize kapenanso kuti ungachite nazo zodabwitsa kwa anthu. 13 Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu opembedza zinthu zakumwamba, oyang’anitsitsa kayendedwe ka nyenyezi,+ amene amalosera zimene zichitike kwa iwe mwezi watsopano ukakhala, tsopano aimirire ndi kukupulumutsa. 14 Iwotu akhala ngati mapesi.+ Moto udzawatentha ndithu.+ Sadzapulumutsa moyo wawo+ ku mphamvu ya moto walawilawi.+ Sudzakhala moto wamakala woti anthu n’kumawotha. Sudzakhala moto wounikira woti anthu n’kuuyandikira. 15 Umu ndi mmene amatsenga+ ako amene wawavutikira kuyambira uli mwana adzakhalire. Iwo adzabalalika, aliyense kulowera kuchigawo cha kwawo ndipo sipadzakhala woti akupulumutse.+
48 Mverani izi inu a m’nyumba ya Yakobo, inu amene mumadzitcha ndi dzina la Isiraeli,+ amene munatuluka kuchokera m’madzi a Yuda,+ amene mumalumbira pa dzina la Yehova,+ ndiponso inu amene mumaitana Mulungu wa Isiraeli,+ koma osati m’choonadi kapena m’chilungamo.+ 2 Pakuti iwo amadzitcha kuti amakhala mumzinda woyera,+ ndipo amadalira Mulungu wa Isiraeli+ amene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+
3 “Ndanena zinthu zoyambirira kuchokera pa nthawi imeneyo. Zinatuluka pakamwa panga, ndipo ndinazichititsa kumveka.+ Mwadzidzidzi, ndinazichita ndipo zinachitikadi.+ 4 Podziwa kuti ndinu olimba,+ ndi kuti mtsempha wa khosi lanu uli ngati chitsulo,+ ndiponso kuti mphumi yanu ili ngati mkuwa,+ 5 ine ndinakuuzani zonse kuyambira nthawi imeneyo. Ndinakuuzani zisanachitike,+ kuti musadzanene kuti, ‘Fano langa ndi limene lachita zimenezi, ndipo chifaniziro changa chosema komanso chifaniziro changa chopangidwa ndi chitsulo chosungunula, n’zimene zalamula zimenezi.’+ 6 Inuyo mwazimva.+ Onani zonsezo.+ Kodi simudzazifotokozera ena?+ Kuyambira panopa ine ndikukuuzani zinthu zatsopano. Ndakuuzani zinthu zobisika zimene simunali kuzidziwa.+ 7 Zinthu zimene ndikulengazi n’zatsopano, si zinthu zakale ayi. Ndi zinthu zimene simunazimvepo m’mbuyomu. Ndikuchita izi chifukwa munganene kuti, ‘Ifetu tinali kuzidziwa kale zimenezi.’+
8 “Komanso, inu simunafune kumva+ kapena kumvetsa zimenezi. Kuyambira pa nthawi imeneyo kupita m’tsogolo, simunatsegule khutu lanu. Pakuti ine ndinkadziwa ndithu kuti inu munali kuchita zachinyengo,+ ndipo mwatchedwa ‘wochimwa chibadwire.’+ 9 Ndidzabweza mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa,+ ndipo chifukwa cha ulemerero wanga, ine ndidzadziletsa kuti ndisakuwonongeni.+ 10 Taonani! Ndinakuyengani koma osati ngati mmene amayengera siliva.+ Ndinakusankhani pamene munali m’ng’anjo ya masautso.+ 11 Ndithu, ndidzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa.+ Pakuti munthu angalekerere bwanji dzina lake likuipitsidwa?+ Ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina aliyense.+
12 “Ndimvere iwe Yakobo, iwe Isiraeli amene ndinakuitana. Ine sindinasinthe.+ Ine ndine woyamba.+ Ndinenso womaliza.+ 13 Komanso dzanja langa linayala maziko a dziko lapansi,+ ndipo dzanja langa lamanja linatambasula kumwamba.+ Ndimafuulira maziko a dziko lapansi ndi kumwamba, kuti ziimirire.+
14 “Sonkhanani pamodzi anthu nonsenu kuti mumve.+ Ndani pakati pawo ananenapo zinthu zimenezi? Iye amene Yehova wamukonda+ adzachitira Babulo zimene akufuna.+ Dzanja lake lidzakhala pa Akasidi.+ 15 Ineyo ndalankhula, komanso ndamuitana.+ Ndamubweretsa, ndipo ndidzachititsa kuti zochita zake zimuyendere bwino.+
16 “Bwerani pafupi ndi ine anthu inu. Mvetserani izi. Kuyambira pa chiyambi, ine sindinalankhulirepo m’malo obisika.+ Pamene zinthu zonenedwazo zinayamba kuchitika, ine ndinalipo.”
Tsopano Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watumiza ine ndiponso watumiza mzimu wake.+ 17 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.+ 18 Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga!+ Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje,+ ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.+ 19 Mbadwa zanu zochokera mkati mwa matupi anu zidzakhala ngati mchenga.+ Dzina lawo silidzatha kapena kuwonongedwa pamaso panga.”+
20 Tulukani m’Babulo anthu inu!+ Thawani m’manja mwa Akasidi.+ Nenani zimenezi ndi mfuu yachisangalalo kuti zimveke.+ Zineneni mokuwa mpaka zimveke kumalekezero a dziko lapansi.+ Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+ 21 Iwo sanamve ludzu+ ngakhale pamene iye anawayendetsa m’chipululu.+ Iye anawatulutsira madzi pathanthwe. Anang’amba thanthwe kuti madzi atulukepo.”+
22 Yehova wanena kuti, “Oipa alibe mtendere.”+
49 Ndimvereni zilumba inu,+ ndipo mvetserani, inu mitundu ya anthu akutali.+ Yehova anandiitana+ ndili m’mimba.+ Ndili mkati mwa mayi anga, anatchula dzina langa.+ 2 Iye anachititsa m’kamwa mwanga kukhala ngati lupanga lakuthwa.+ Anandibisa mumthunzi+ wa dzanja lake.+ Anandisandutsa muvi wonola bwino. Anandibisa m’kachikwama kake koikamo mivi. 3 Kenako anandiuza kuti: “Iwe Isiraeli ndiwe mtumiki wanga.+ Ine ndidzaonetsera kukongola kwanga pa iwe.”+
4 Koma ine ndinati: “Ndangovutika pachabe.+ Mphamvu zanga ndangoziwonongera zinthu zopanda pake ndi zachabechabe.+ Ndithu, Yehova ndiye amene adzandiweruze+ ndipo Mulungu wanga ndiye amene adzandipatse mphoto yanga.”+ 5 Tsopano Yehova, amene anandipanga ndili m’mimba kuti ndikhale mtumiki wake,+ wanena kuti ndimubwezere Yakobo,+ n’cholinga choti Isiraeli asonkhanitsidwe kwa iye.+ Ine ndidzakhala wolemekezeka pamaso pa Yehova ndipo Mulungu wanga adzakhala mphamvu yanga. 6 Ndiyeno iye anati: “Si nkhani yochepa kuti iweyo wakhala mtumiki wanga, n’cholinga choti ubwezeretse mafuko a Yakobo ndi kubweza Aisiraeli amene ali otetezeka.+ Ndakupereka kuti ukhale kuwala kwa mitundu ya anthu,+ kuti chipulumutso changa chifike mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”+
7 Yehova, Wowombola Isiraeli,+ Woyera wake, wauza yemwe ananyozedwa kwambiri,+ yemwe amadedwa ndi mtundu wa anthu,+ mtumiki wa atsogoleri,+ kuti: “Mafumu adzaimirira chifukwa cha zimene adzaone,+ ndipo akalonga adzagwada chifukwa cha Yehova. Iye ndi wokhulupirika,+ Woyera wa Isiraeli, amene anakusankha.”+
8 Yehova wanena kuti: “Pa nthawi yapadera yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha.+ M’tsiku la chipulumutso, ndinakuthandiza.+ Ndinakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,+ kuti ndikonzenso dzikolo,+ kuti anthu ayambirenso kukhala m’cholowa chawo chimene chinali bwinja,+ 9 kuti ndiuze akaidi+ kuti, ‘Tulukani!’+ ndi amene ali mu mdima+ kuti, ‘Dziululeni!’+ Iwo adzadya msipu m’mphepete mwa msewu, ndipo m’mphepete mwa njira zonse zodutsidwadutsidwa mudzakhala malo awo odyeramo msipu.+ 10 Iwo sadzakhala ndi njala+ ndipo sadzamva ludzu.+ Sadzamva kutentha kapena kupsa ndi dzuwa.+ Pakuti yemwe amawamvera chisoni adzawatsogolera+ ndipo adzapita nawo ku akasupe amadzi.+ 11 Ndidzachititsa kuti mapiri anga onse akhale njira, ndipo misewu yanga yonse idzakhala pamalo okwera.+ 12 Taonani! Awa adzachokera kutali,+ ndipo awa adzachokera kumpoto+ ndi kumadzulo.+ Awanso adzachokera kudziko la Sinimu.”
13 Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ ndipo sangalala iwe dziko lapansi.+ Mapiri asangalale ndipo afuule ndi chisangalalo.+ Pakuti Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo amamvera chisoni anthu ake osautsidwa.+
14 Koma Ziyoni ankangonena kuti: “Yehova wandisiya+ ndipo Yehova wandiiwala.”+ 15 Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa, osamvera chisoni mwana wochokera m’mimba mwake?+ Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala,+ koma ine sindidzakuiwala.+ 16 Taona! Ndakudinda m’manja mwanga.+ Makoma ako ali pamaso panga nthawi zonse.+ 17 Ana ako abwera mofulumira. Anthu amene anali kukukhadzula ndi kukuwononga adzakuchokera. 18 Takweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse asonkhanitsidwa pamodzi.+ Abwera kwa iwe. Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,+ onsewo udzadzikongoletsa nawo ngati zokongoletsera, ndipo udzawavala ngati ndiwe mkwatibwi.+ 19 Ngakhale kuti panopa malo ako ndi owonongeka, osakazidwa ndiponso abwinja,+ ngakhale kuti panopa malo ako ndi osatakasuka mokwanira kuti n’kukhalamo bwinobwino, ndipo okumeza akhala kutali,+ 20 koma ana ako amene unabereka ana ena onse atamwalira,+ adzakuuza kuti, ‘Malowa atichepera.+ Tipezereni malo oti tikhalemo.’+ 21 Iweyo udzanenadi mumtima mwako kuti, ‘Kodi bambo wa ana amene ndaberekawa ndani, popeza ine ndine mayi woferedwa ana ndiponso wosabereka, mayi yemwe anatengedwa kupita kudziko lina ku ukaidi?+ Nanga ana awa, anawalera ndani?+ Inetu ndinasiyidwa m’mbuyo ndekhandekha.+ Ndiyeno ana awa anali kuti?’”+
22 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Taona! Ineyo ndidzakwezera dzanja langa mitundu ya anthu,+ ndipo anthu a mitundu yosiyanasiyana ndidzawakwezera chizindikiro.+ Iwo adzakubweretsera ana ako aamuna atawanyamulira pachifuwa, ndipo ana ako aakazi adzawanyamulira paphewa.+ 23 Mafumu adzakhala okusamalira,+ ndipo ana awo aakazi adzakhala okuyamwitsira ana ako. Iwo adzakugwadira mpaka nkhope zawo pansi+ ndipo adzanyambita fumbi la kumapazi ako.+ Pamenepo, ndithu iweyo udzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndiponso kuti anthu okhulupirira mwa ine sadzachita nane manyazi.”+
24 Kodi anthu amene atengedwa kale angalandidwe m’manja mwa munthu wamphamvu,+ kapena kodi gulu la anthu amene agwidwa ndi wolamulira wankhanza lingathawe?+ 25 Koma Yehova wanena kuti: “Ngakhale gulu la anthu ogwidwa ndi munthu wamphamvu lidzatengedwa,+ ndipo amene anatengedwa kale ndi wolamulira wankhanza adzathawa.+ Aliyense wolimbana nawe, ineyo ndidzalimbana naye,+ ndipo ana ako ndidzawapulumutsa.+ 26 Amene akukuzunza ndidzawachititsa kuti adye mnofu wawo womwe, ndipo adzaledzera ndi magazi awo omwe ngati kuti amwa vinyo wotsekemera. Anthu onse ndithu adzadziwa kuti ine, Yehova,+ ndine Mpulumutsi wako+ ndiponso Wokuwombola,+ Wamphamvu wa Yakobo.”+
50 Yehova wanena kuti: “Kodi anthu inu, chili kuti chikalata chothetsera ukwati+ wa mayi wanu yemwe ndinamuthamangitsa?+ Kapena kodi anthu inu ndakugulitsani+ kwa munthu uti amene ndinali naye ngongole? Inutu mwagulitsidwa chifukwa cha zolakwa zanu,+ ndipo mayi wanu wathamangitsidwa chifukwa cha zochimwa zanu.+ 2 N’chifukwa chiyani nditabwera sindinapeze aliyense?+ N’chifukwa chiyani nditaitana palibe amene anayankha?+ Kodi dzanja langa lafupika kwambiri moti silingathe kuwombola,+ kapena kodi mwa ine mulibe mphamvu zopulumutsira? Inetu ndimaumitsa nyanja+ pongoidzudzula chabe.+ Mitsinje ndimaisandutsa chipululu.+ Nsomba zake zimanunkha chifukwa chakuti mulibe madzi ndipo zimafa ndi ludzu.+ 3 Kumwamba ndimakuveka mdima+ ndipo chiguduli ndimachisandutsa chophimba chake.”+
4 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wandipatsa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino+ kuti ndidziwe mmene ndingamuyankhire munthu wotopa.+ Iye amandidzutsa m’mawa uliwonse. Amandidzutsa kuti makutu anga amve ngati anthu ophunzitsidwa bwino.+ 5 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanditsegula khutu ndipo ineyo sindinapanduke.+ Sindinatembenukire kwina.+ 6 Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya, ndipo masaya anga+ ndinawapereka kwa ozula ndevu. Nkhope yanga sindinaitchinjirize kuti isachitidwe zinthu zamanyazi ndi kulavuliridwa.+
7 Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza.+ N’chifukwa chake sindidzamva kuti ndanyozeka. Pa chifukwa chimenechi ndalimbitsa nkhope yanga ngati mwala wa nsangalabwi, ndipo ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.+ 8 Amene adzanene kuti ndine wolungama ali pafupi.+ Ndani angalimbane nane? Tiyeni tikaonane pabwalo lamilandu.+ Kodi wotsutsana nane pa mlandu ndani?+ Abwere kufupi.+ 9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza. Ndani amene anganene kuti ndine wolakwa?+ Onsewo adzatha ngati chovala.+ Njenjete* idzawadya.+
10 Ndani pakati panu amene amaopa+ Yehova ndi kumvera mawu a mtumiki wake?+ Ndani amayenda mu mdima wokhawokha+ ndipo alibe kuwala? Iye akhulupirire dzina la Yehova+ ndipo adalire Mulungu wake.+
11 “Inu nonse amene mukuyatsa moto, amene mukuchititsa kuti uziwala n’kumathetheka, yendani m’kuwala kwa moto wanu, ndipo yendani pakati pa malawi a moto wothetheka umene mwayatsawo. Mudzalandira izi kuchokera m’dzanja langa: Mudzagona pansi mukumva ululu woopsa.+
51 “Ndimvereni, inu anthu amene mukufunafuna chilungamo,+ inu amene mukufuna kupeza Yehova.+ Yang’anani kuthanthwe+ limene munasemedwako, ndi kuphanga la dzenje limene munakumbidwako. 2 Yang’anani kwa tate+ wanu Abulahamu,+ ndi kwa Sara+ amene anakuberekani ndi zowawa za pobereka. Abulahamuyo anali munthu mmodzi pamene ndinamuitana,+ koma ndinamudalitsa ndi kumusandutsa anthu ambiri.+ 3 Pakuti Yehova adzatonthoza Ziyoni.+ Iye adzatonthozadi malo ake onse owonongedwa.+ Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+ ndi dera lake lachipululu kukhala ngati munda wa Yehova.+ Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera, kuyamikira ndi kuimba nyimbo.+
4 “Inu anthu anga, tandimverani. Iwe mtundu wanga,+ tatchera khutu kwa ine. Pakuti kwa ine kudzachokera lamulo+ ndipo ndidzachititsa chigamulo changa kukhazikika monga kuwala kwa mitundu ya anthu.+ 5 Chilungamo changa chili pafupi.+ Chipulumutso+ chochokera kwa ine chili m’njira ndipo manja anga adzaweruza mitundu ya anthu.+ Zilumba zidzayembekezera ine+ ndipo zidzadikira dzanja langa.+
6 “Kwezani maso anu kumwamba,+ ndipo yang’anani padziko lapansi. Pakuti kumwamba kudzabenthukabenthuka n’kumwazidwa ngati utsi,+ ndipo dziko lapansi lidzatha ngati chovala.+ Anthu okhalamo adzafa ngati ntchentche. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka kalekale+ ndipo chilungamo changa sichidzaphwanyika.+
7 “Ndimvereni, inu odziwa chilungamo, inu amene muli ndi lamulo langa mumtima mwanu.+ Musaope chitonzo cha anthu ndipo musachite mantha chifukwa cha mawu awo onyoza.+ 8 Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala ndipo kachilombo kodya zovala kadzawadya ngati thonje.+ Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka kalekale ndipo chipulumutso changa chidzafikira mibadwo yosawerengeka.”+
9 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu,+ iwe dzanja la Yehova!+ Dzuka ngati masiku akale, ngati m’mibadwo yakalekale.+ Kodi si iwe amene unaphwanyaphwanya Rahabi,+ amene unabaya* chilombo cha m’nyanja?+ 10 Kodi si iwe amene unaumitsa nyanja, amene unaumitsa madzi akuya kwambiri?+ Si iwe kodi amene unasandutsa pansi pa nyanja kukhala njira yoti anthu owomboledwa awolokerepo?+ 11 Chotero, owomboledwa a Yehova adzabwerera ku Ziyoni ndi mfuu yachisangalalo,+ ndipo pamutu pawo padzakhala chisangalalo mpaka kalekale.+ Iwo adzapeza chisangalalo ndi chimwemwe.+ Chisoni ndi kuusa moyo zidzachoka.+
12 “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.+
“Kodi n’chifukwa chiyani iwe ukuopa munthu woti adzafa,+ ndi mwana wa munthu yemwe adzakhale ngati udzu wobiriwira?+ 13 Kodi n’chifukwa chiyani ukuiwala Yehova amene anakupanga,+ amene anatambasula kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi?+ N’chifukwa chiyani ukuchita mantha nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu, poopa mkwiyo wa yemwe akukupanikizira mkati,+ ngati kuti iye wakonzeka kuti akuwononge?+ Kodi mkwiyo wa amene akukupanikizira mkati uli kuti?+
14 “Yemwe wawerama atamangidwa maunyolo adzamasulidwa msangamsanga.+ Iye sadzafa, sadzatsikira kudzenje,+ komanso sadzasowa chakudya.+
15 “Koma ine Yehova ndine Mulungu wako, amene ndimavundula nyanja kuti mafunde ake achite phokoso.+ Yehova wa makamu ndiye dzina langa.+ 16 Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwako+ ndipo ndidzakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa.+ Ndidzachita zimenezi n’cholinga choti ndikhazikitse kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi,+ ndiponso kuti ndiuze Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’+
17 “Dzuka! Dzuka! Imirira iwe Yerusalemu,+ iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo wa Yehova kuchokera m’dzanja lake.+ Iweyo wamwa ndipo wagugudiza chipanda, chikho chochititsa munthu kuyenda dzandidzandi.+ 18 Pa ana onse amene iye anabereka, palibe ndi mmodzi yemwe+ amene anali kutsogolera mayiyo poyenda. Pa ana onse amene iye analera, palibe ndi mmodzi yemwe amene anagwira dzanja lake.+ 19 Zinthu ziwiri zidzakugwera.+ Kodi adzakumvera chisoni ndani?+ Udzalandidwa katundu ndi kuphwanyidwa, ndiponso udzakumana ndi njala ndi lupanga.+ Kodi adzakutonthoza ndani?+ 20 Ana ako akomoka.+ Agona m’misewu yonse ngati nkhosa zakutchire zokodwa mu ukonde,+ ngati anthu okhuta mkwiyo wa Yehova,+ okhuta kudzudzula kwa Mulungu wako.”+
21 Chotero mvetsera izi, iwe mkazi+ wosautsidwa ndi woledzera, koma osati ndi vinyo.+ 22 Ambuye wako, Yehova, Mulungu wako, amene amateteza+ anthu ake, wanena kuti: “Taona! Ine ndidzachotsa m’manja mwako chikho chochititsa munthu kudzandira.+ Sudzamwanso chipanda, chikho cha mkwiyo wanga.+ 23 Ndidzachiika m’manja mwa amene akukuvutitsa,+ amene akukuuza kuti, ‘Werama kuti tiwolokere pamsana pako,’ amene akuona msana wako ngati pansi popondapo, ndiponso ngati njira yowolokerapo.”+
52 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu zako+ iwe Ziyoni. Vala zovala zako zokongola+ iwe Yerusalemu, mzinda woyera.+ Pakuti mwa iwe simudzabweranso munthu wosadulidwa ndi wodetsedwa.+ 2 Dzuka pafumbi pamene ulipo.+ Sansa fumbilo, khala pamalo aulemu iwe Yerusalemu. Masula zingwe zimene zili m’khosi mwako, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni wogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+
3 Pakuti Yehova wanena kuti: “Anthu inu munagulitsidwa popanda malipiro alionse,+ ndipo mudzawomboledwanso popanda ndalama.”+
4 Pakuti Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Poyamba anthu anga anapita ku Iguputo kuti akakhale ngati alendo.+ Ndiyeno Asuri anawapondereza popanda chifukwa.”
5 “Tsopano kodi pamenepa ndichitepo chiyani?” akutero Yehova. “Pakuti anthu anga anatengedwa popanda malipiro alionse.+ Amene anali kuwalamulira ankangokhalira kufuula.+ Nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu, dzina langa anali kulichitira chipongwe,”+ akutero Yehova. 6 “Pa chifukwa chimenecho anthu anga adzadziwa dzina langa.+ Adzalidziwa pa chifukwa chimenecho m’tsiku limenelo, pakuti ineyo ndi amene ndikulankhula.+ Ndithu ndineyo.”
7 Mapazi+ a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino, ndi okongola kwabasi!+ Munthu yemwe akulengeza za mtendere,+ yemwe akubweretsa uthenga wabwino wa zinthu zabwino kuposa kale,+ yemwe akulengeza za chipulumutso,+ yemwe akuuza Ziyoni kuti: “Mulungu wako wakhala mfumu.”+
8 Tamvera! Alonda ako+ akufuula.+ Onse akufuula pamodzi mokondwera. Pamene Yehova azidzasonkhanitsanso okhala mu Ziyoni,+ iwo adzaona ndi maso awo.+
9 Inu malo osakazidwa a mu Yerusalemu, sangalalani nonse pamodzi ndipo fuulani mokondwa,+ pakuti Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo wawombola Yerusalemu.+ 10 Yehova waika pamtunda dzanja lake loyera kuti mitundu yonse ione,+ ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.+
11 Tembenukani! Tembenukani! Tulukani mmenemo!+ Musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa.+ Chokani pakati pake!+ Khalani oyera, inu amene mukunyamula ziwiya za Yehova.+ 12 Anthu inu simudzatuluka mwachipwirikiti, komanso simudzachoka chothawa.+ Pakuti Yehova azidzayenda patsogolo panu,+ ndipo Mulungu wa Isiraeli azidzalondera kumbuyo kwanu.+
13 Taona! Mtumiki wanga+ azidzachita zinthu mwanzeru.+ Iye adzakhala ndi udindo wapamwamba ndipo adzakwezedwa ndi kulemekezedwa kwambiri.+ 14 Monga momwe anthu ambiri anamuyang’anira modabwa,+ pakuti nkhope yake inali yoipa kwambiri+ kuposa ya munthu wina aliyense, ndiponso maonekedwe ake+ anali oipa kuposa a ana a anthu, 15 momwemonso iye adzadabwitsa mitundu yambiri.+ Mafumu adzatseka pakamwa pawo akadzamuona,+ chifukwa iwo adzaona zimene sanauzidwepo, ndipo adzaganizira zimene sanamvepo.+
53 Kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva?+ Ndipo kodi dzanja la Yehova+ laonetsedwa kwa ndani?+ 2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pa winawake, ndiponso ngati muzu m’dziko lopanda madzi. Alibe maonekedwe alionse apamwamba kapena okongola,+ ndipo maonekedwe ake si osiririka m’maso mwathu.+
3 Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+ 4 Zoonadi, iye anatinyamulira matenda athu+ ndipo anatisenzera zowawa zathu.+ Koma ifeyo tinamuona ngati wosautsidwa,+ wokwapulidwa ndi Mulungu,+ ndiponso wozunzidwa.+ 5 Iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+ Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+ Chilango chotibweretsera mtendere chinam’gwera iyeyo,+ ndipo chifukwa cha zilonda zake+ ifeyo tachiritsidwa.+ 6 Tonsefe tinkangoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa.+ Aliyense analowera njira yake ndipo Yehova wachititsa cholakwa cha aliyense wa ife kugwera pa ameneyo.+ 7 Iye anapanikizidwa+ ndipo analola kuti asautsidwe,+ koma sanatsegule pakamwa pake. Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa,+ ndipo mofanana ndi nkhosa yaikazi imene imakhala chete akamaimeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+
8 Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.+ Ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo ake?+ Pakuti iye anadulidwa+ m’dziko la amoyo.+ Chifukwa cha zolakwa+ za anthu anga, iye anakwapulidwa.+ 9 Manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa,+ ndipo adzakhala limodzi ndi anthu olemera pa imfa yake,+ ngakhale kuti iye sanachite zachiwawa zilizonse+ ndipo m’kamwa mwake munalibe chinyengo.+
10 Koma zinamukomera Yehova kuti mtumiki wake aphwanyidwe.+ Iye anamulola kuti adwale.+ Mukapereka moyo wake monga nsembe ya kupalamula,+ iye adzaona ana ake.+ Adzatalikitsa masiku ake+ ndipo ndi dzanja lake, adzakwaniritsa zokonda+ Yehova.+ 11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino+ ndipo adzakhutira.+ Chifukwa cha zimene akudziwa, mtumiki wanga wolungamayo+ adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+ ndipo adzasenza zolakwa zawo.+ 12 Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri+ ndipo iye adzagawana zolanda ndi amphamvu,+ chifukwa anakhuthula moyo wake mu imfa+ ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa.+ Iye ananyamula tchimo la anthu ambiri+ ndipo analowererapo kuti athandize olakwa.+
54 “Iwe mkazi wosabereka amene sunaberekepo mwana,+ fuula mokondwa!+ Iwe amene sunamvepo zowawa za pobereka,+ kondwera! Fuula mokondwa! Kuwa ndi chisangalalo, pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi yemwe ali ndi mwamuna,”+ watero Yehova. 2 “Kulitsa hema wako.+ Nsalu za hema wako wamkulu zitambasulidwe. Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za hema wako ndipo ulimbitse zikhomo zake.+ 3 Pakuti iwe udzafutukukira mbali ya kudzanja lamanja ndi kumanzere, ndipo ana ako+ adzalanda ngakhale mitundu ya anthu.+ Iwo adzakhala m’mizinda imene inasiyidwa yabwinja.+ 4 Usachite mantha,+ pakuti sudzachititsidwa manyazi.+ Usachite manyazi, pakuti sudzakhumudwitsidwa.+ Iwe udzaiwala ngakhale manyazi a paubwana wako,+ ndipo sudzakumbukiranso kunyozeka kwa paumasiye wako wa nthawi yaitali.”
5 “Pakuti Wokupanga Wamkulu+ ndiye mwamuna wako.+ Dzina lake ndi Yehova wa makamu,+ ndipo Woyera wa Isiraeli ndiye Wokuwombola.+ Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.+ 6 Yehova anakuitana ngati kuti unali mkazi wosiyidwa mpaka kalekale ndi wopwetekedwa mumtima,+ ndiponso ngati mkazi wa paunyamata+ amene kenako anadzasiyidwa,”+ watero Mulungu wako.
7 “Kwa kanthawi kochepa ndinakusiyiratu,+ koma ndidzakusonkhanitsa pamodzi mwachifundo chachikulu.+ 8 Ndi mkwiyo waukulu ndinakubisira nkhope yanga kwa kanthawi,+ koma ndidzakuchitira chifundo+ ndiponso ndidzakusonyeza kukoma mtima kosatha mpaka kalekale,” watero Yehova, Wokuwombola.+
9 “Kwa ine, zimenezi zili ngati masiku a Nowa.+ Monga mmene ndinalumbirira kuti madzi a Nowa sadzadutsanso padziko lapansi,+ momwemonso ndalumbira kuti sindidzakukwiyira kapena kukudzudzula.+ 10 Pakuti mapiri akhoza kuchotsedwa, ndipo zitunda zikhoza kugwedezeka,+ koma kukoma mtima kwanga kosatha sikudzachotsedwa kwa iwe,+ ndipo pangano langa la mtendere silidzagwedezeka,”+ watero Yehova, amene akukuchitira chifundo.+
11 “Iwe mkazi wosautsidwa,+ wokankhidwakankhidwa ndi mphepo yamkuntho,+ ndiponso wosatonthozedwa,+ ine ndikumanga miyala yako ndi simenti yolimba,+ ndipo ndidzayala maziko ako+ ndi miyala ya safiro.+ 12 Nsanja za pamakoma ako ndidzazimanga ndi miyala ya rube, ndipo zipata zako ndidzazimanga ndi miyala yofiira ngati moto.+ Zizindikiro za m’malire ako onse ndidzazimanga ndi miyala yamtengo wapatali. 13 Ana ako onse+ adzakhala anthu ophunzitsidwa ndi Yehova,+ ndipo mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka.+ 14 Iwe udzakhazikika m’chilungamo.+ Kuponderezedwa udzatalikirana nako,+ ndipo sudzaopa aliyense. Chilichonse choopsa udzatalikirana nacho, pakuti sichidzakuyandikira.+ 15 Ngati aliyense atakuukira, sadzakhala atatumidwa ndi ine.+ Aliyense wokuukira adzagwa chifukwa cha iwe.”+
16 “Inetu ndi amene ndinalenga mmisiri, amene amauzira+ moto wamakala+ n’kupanga chida chankhondo ndi luso lake. Inenso ndi amene ndinalenga munthu wowononga,+ amene amagwira ntchito yowononga ena. 17 Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana,+ ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa.+ Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova,+ ndipo chilungamo chawo n’chochokera kwa ine,” akutero Yehova.+
55 Inu nonse amene mukumva ludzu,+ bwerani mudzamwe madzi.+ Inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule kuti mudye.+ Inde bwerani mudzagule vinyo+ ndi mkaka+ popanda ndalama ndiponso popanda mtengo wake.+ 2 N’chifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya, ndipo n’chifukwa chiyani mukuvutika kugwirira ntchito zinthu zimene sizikhutitsa?+ Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino,+ ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.+ 3 Tcherani khutu+ lanu ndipo bwerani kwa ine.+ Mvetserani ndipo mudzakhalabe ndi moyo.+ Ine ndidzachita nanu pangano lokhalapo mpaka kalekale+ lokhudza kukoma mtima kwanga kosatha kosonyezedwa kwa Davide, kumene kuli kokhulupirika.+ 4 Taonani! Ine ndamupereka+ iye monga mboni+ kwa mitundu ya anthu,+ ndiponso monga mtsogoleri+ ndi wolamulira+ wa mitundu ya anthu.
5 Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,+ ndipo anthu a mtundu wosakudziwa adzathamangira kwa iwe+ chifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ ndiponso chifukwa cha Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakukongoletsa.+
6 Anthu inu funafunani Yehova pamene iye akupezekabe.+ Muitaneni akadali pafupi.+ 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+
8 “Maganizo a anthu inu si maganizo anga,+ ndipo njira zanga si njira zanu,”+ akutero Yehova. 9 “Pakuti monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi,+ momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu,+ ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.+ 10 Pakuti monga momwe mvula ndi chipale chofewa zimagwera kuchokera kumwamba, osabwereranso kumeneko mpaka zitanyowetsa kwambiri nthaka n’kumeretsa zomera ndi kuzibereketsa,+ wobzala mbewu n’kupatsidwa zokolola komanso wakudya n’kupatsidwa chakudya,+ 11 ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+
12 “Pakuti anthu inu mudzachoka ndi chisangalalo+ ndipo mudzafika ndi mtendere.+ Mapiri ndi zitunda zidzakusangalalirani ndi mfuu yachisangalalo,+ ndipo mitengo yonse yakutchire idzawomba m’manja.+ 13 M’malo mwa chitsamba chaminga padzamera mtengo wa mkungudza.+ M’malo mwa chomera choyabwa padzamera mtengo wa mchisu.+ Zimenezi zidzamutchukitsa Yehova,+ ndipo zidzakhala chizindikiro choti sichidzachotsedwa mpaka kalekale.”+
56 Yehova wanena kuti: “Anthu inu, tsatirani chilungamo+ ndipo chitani zolungama.+ Pakuti chipulumutso changa chatsala pang’ono kubwera,+ ndipo chilungamo changa chatsala pang’ono kuonekera.+ 2 Wodala ndi munthu amene amachita zimenezi,+ ndiponso mwana wa munthu amene amatsatira zimenezi,+ amene amasunga sabata kuti asalidetse,+ ndiponso amaletsa dzanja lake kuti lisachite choipa chilichonse.+ 3 Mlendo yemwe wadziphatika kwa Yehova asanene kuti,+ ‘Ndithu Yehova adzandilekanitsa ndi anthu ake.’+ Nayenso munthu wofulidwa+ asanene kuti, ‘Ine ndiye ndine mtengo wouma basi.’”
4 Pakuti Yehova wanena kuti: “Anthu ofulidwa amene amasunga sabata langa, ndiponso amene asankha kuchita zimene ndimasangalala nazo,+ komanso amene amatsatira pangano langa,+ 5 m’nyumba mwanga+ ndiponso mkati mwa makoma anga ndidzawapatsa chipilala chachikumbutso+ ndiponso dzina,+ zomwe ndi zabwino kuposa ana aamuna ndi aakazi.+ Ndidzawapatsa dzina limene silidzatha+ mpaka kalekale.+
6 “Alendo amene adziphatika kwa Yehova kuti am’tumikire+ ndiponso amene amakonda dzina la Yehova+ n’cholinga choti akhale atumiki ake, onse amene amasunga sabata kuti asalidetse ndiponso amene amatsatira pangano langa,+ 7 ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+ ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo.+ Nsembe zawo zopsereza zathunthu+ ndi nsembe zawo zina+ ndidzazilandira paguwa langa lansembe.+ Pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+
8 Mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, amene akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli omwe anabalalitsidwa,+ ndi akuti: “Ine ndidzamusonkhanitsiranso anthu ena kuwonjezera pa anthu ake amene anasonkhanitsidwa kale.”+
9 Inu nyama zonse zakutchire, inu nyama zonse za m’nkhalango, bwerani mudzadye.+ 10 Alonda ake ndi akhungu+ ndipo sakudziwa chilichonse.+ Onsewo ndi agalu opanda mawu. Satha kuuwa.+ Amangokhalira kupuma wefuwefu ndi kugona pansi. Amakonda kugona tulo.+ 11 Iwo ndi agalu adyera kwambiri+ ndipo sakhuta,+ komanso ndi abusa osamvetsa zinthu.+ Aliyense wa iwo wapatukira kunjira yake n’cholinga chopeza phindu lachinyengo lochokera m’dera lake.+ Iwo amati: 12 “Tabwerani amuna inu! Dikirani kaye ndikatenge vinyo. Timwe mpaka kuledzera.+ Mawa lidzakhalanso ngati lero, mwinanso kuposa pamenepa.”+
57 Wolungama wawonongedwa,+ koma palibe amene zikum’khudza.+ Anthu amene amasonyeza kukoma mtima kosatha akusonkhanitsidwira kwa akufa+ popanda wozindikira kuti munthu wolungamayo wafa ndipo wathawa tsoka.+ 2 Iye amalowa mumtendere.+ Aliyense woyenda mowongoka+ amapita kukapuma+ m’manda.*+
3 “Koma anthu inu bwerani pafupi,+ inu ana a mayi wolosera zam’tsogolo,+ mbewu ya munthu wachigololo ndi ya mkazi wochita uhule:+ 4 Kodi mukusangalala chifukwa cha kuvutika kwa ndani?+ Kodi mukuyasamulira ndani pakamwa panu, ndi kum’tulutsira lilime?+ Kodi inu si inu ana a machimo, mbewu ya chinyengo,+ 5 amene mumadzutsa chilakolako chanu pakati pa mitengo ikuluikulu+ ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+ Kodi si inu amene mumapha ana m’zigwa* pakati pa matanthwe?+
6 “Gawo lako linali pamodzi ndi miyala yosalala ya m’chigwa.+ Iwo ndiwo anali gawo lako.+ Iwe unawathirira nsembe yachakumwa,+ ndiponso unawapatsa mphatso. Kodi ine ndingadzitonthoze ndi zinthu zimenezo?+ 7 Bedi lako unaliika pamwamba pa phiri lalitali ndi lokwezeka.+ Unapitanso kumeneko kukapereka nsembe.+ 8 Unaika chizindikiro chachikumbutso chako kuseri kwa chitseko ndi kuseri kwa felemu.+ Iwe unavula n’kukwera mtunda kupita kumeneko uli kutali ndi ine. Unakulitsa bedi lako,+ ndipo unachita nawo pangano. Unkakonda kugona nawo pabedi+ ndipo unaona chiwalo cha mwamuna. 9 Iwe unatsetserekera kwa Meleki utatenga mafuta, ndipo unachulukitsa mafuta ako onunkhira.+ Unapitiriza kutumiza nthumwi zako kutali kwambiri moti mpaka unatsitsira zochita zako m’Manda.+ 10 Wakhala ukugwira ntchito mwamphamvu m’njira zako zambirimbiri.+ Sunanene kuti, ‘N’zopanda phindu!’ Wapezanso mphamvu zina.+ N’chifukwa chake sunadwale.+
11 “Kodi unachita mantha ndi ndani kuti uyambe kuopa,+ mpaka kuyamba kunama?+ Koma sunakumbukire ine.+ Palibe chimene unaganizira mumtima mwako.+ Popeza ine ndinakhala chete ndipo sindinachitepo kanthu pa zochita zako,+ iweyo sunali kundiopa.+ 12 Ineyo ndidzanena za chilungamo chako+ ndi ntchito zako,+ kuti sizidzakupindulira.+ 13 Ukamafuula popempha thandizo, zinthu zimene unasonkhanitsa sizidzakupulumutsa,+ koma mphepo idzaziulutsa zonsezo+ ndipo mpweya udzazitenga. Koma munthu wobisala mwa ine+ adzalandira dziko ndipo adzatenga phiri langa loyera.+ 14 Ndiyeno wina adzati, ‘Anthu inu, konzani msewu! Konzani msewu anthu inu! Lambulani msewu.+ Chotsani chopinga chilichonse panjira ya anthu anga.’”+
15 Pakuti Wapamwamba ndi Wokwezeka,+ yemwe adzakhalepo kwamuyaya+ ndiponso yemwe dzina lake ndi loyera,+ wanena kuti: “Ine ndimakhala kumwamba pamalo oyera.+ Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa,+ kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.+ 16 Pakuti ine sindidzatsutsana nanu mpaka kalekale, ndiponso sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.+ Popeza chifukwa cha ine, mzimu wa munthu ukhoza kufooka,+ ngakhalenso zinthu zopuma zimene ineyo ndinapanga.+
17 “Ine ndinakwiya chifukwa cha phindu lachinyengo limene analipeza mosayenera.+ Ndinakwiya ndipo ndinamulanga. Ndinabisa nkhope yanga chifukwa cha mkwiyo.+ Koma iye ankangoyendabe ngati wopanduka+ m’njira ya mtima wake. 18 Ine ndaona njira zake. Ndinayamba kumuchiritsa+ ndi kumutsogolera,+ ndiponso ndinamutonthoza+ iyeyo ndi anthu ake amene anali kulira.”+
19 “Ndikulenga chipatso cha milomo.+ Mtendere wosatha udzakhala kwa yemwe ali kutali ndiponso kwa yemwe ali pafupi,+ ndipo ndidzam’chiritsa,”+ akutero Yehova.
20 “Koma anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuwinduka, imene ikukanika kukhala bata, imene madzi ake akuvundula zomera za m’nyanjamo ndiponso matope. 21 Oipa alibe mtendere,”+ akutero Mulungu wanga.
58 “Fuula mwamphamvu! Usabweze mawu.+ Kweza mawu ako ngati lipenga,+ ndipo uza anthu anga za kupanduka kwawo. A nyumba ya Yakobo uwauze machimo awo. 2 Koma tsiku ndi tsiku iwo anali kufunafuna ineyo. Anali kunena kuti amasangalala kudziwa njira zanga,+ ngati mtundu umene unali kuchita zolungama ndiponso ngati mtundu umene sunasiye chilungamo cha Mulungu wawo.+ Iwo ankangokhalira kundipempha chiweruzo cholungama, ndipo anali kuyandikira kwa Mulungu amene anali kumukonda.+
3 Tsopano iwo akunena kuti: “‘Kodi ifeyo tinavutikiranji kusala kudya inu osaona,+ ndipo tinadzisautsiranji+ inu osasamala n’komwe?’+
“Komatu anthu inu munali kusangalala tsiku limene munali kusala kudya, pamene antchito anu onse munali kuwagwiritsa ntchito yakalavulagaga.+ 4 Ndithu inuyo munali kusala kudya n’cholinga choti muzikangana, kulimbana,+ ndiponso kuti muzimenyana ndi nkhonya zovulaza.+ Kodi inuyo simunali kusala kudya n’kumaganiza kuti inali nthawi yoti mawu anu amveke kumwamba? 5 Kodi kusala kudya kumene ine ndasankha kukhale kotere? Kodi likhale tsiku loti munthu wochokera kufumbi azisautsa moyo wake?+ Kodi likhale tsiku loti munthu aziweramitsa mutu wake ngati udzu, ndiponso loti aziyala chiguduli ngati bedi lake n’kuwazapo phulusa?+ Kodi limeneli ndi limene mumalitcha tsiku losala kudya ndi lovomerezeka kwa Yehova?+
6 “Kusala kudya kumene ine ndimafuna n’kotere: Mumasule maunyolo ozunzira anzanu,+ mumasule zingwe za goli,+ mumasule anthu opsinjika kuti azipita kwawo,+ ndipo goli lililonse mulithyole pakati.+ 7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+ ndiponso kuti muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala.+ Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka+ ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.+
8 “Mukatero kuwala kwanu kudzaonekera ngati m’bandakucha,+ ndipo mudzachira mofulumira kwambiri.+ Chilungamo chanu chizidzayenda patsogolo panu,+ ndipo ulemerero wa Yehova uzidzalondera kumbuyo kwanu.+ 9 Chotero inu mudzaitana ndipo Yehova adzakuyankhani. Mudzafuula popempha+ ndipo iye adzayankha kuti, ‘Ndikumva lankhulani!’
“Mukachotsa goli pakati panu,+ mukaleka kutosana chala+ ndi kulankhulana zopweteka,+ 10 mukapatsa munthu wanjala zinthu zimene inuyo mumakonda,+ ndiponso mukakhutiritsa munthu amene akusautsidwa, kuunika kwanu kudzawala kuti ngwee! mu mdima, ndipo mdima wanu udzakhala ngati masana dzuwa likakhala paliwombo.+ 11 Yehova azidzakutsogolerani+ nthawi zonse+ ndipo adzakukhutiritsani ngakhale m’dziko louma.+ Iye adzatsitsimula mafupa anu+ ndipo inu mudzakhala ngati munda wachinyontho chokwanira bwino,+ ndiponso ngati kasupe wamadzi yemwe madzi ake sanama. 12 Chifukwa cha inu, anthu adzamanga malo amene anawonongedwa kalekale.+ Inu mudzamanganso maziko amene akhalapo ku mibadwomibadwo.+ Mudzatchedwa otseka mipata ya mpanda,+ ndiponso okonzanso misewu yomwe anthu amakhala m’mphepete mwake.
13 “Mukabweza phazi lanu chifukwa cha sabata, kuti musiye kuchita zokonda zanu pa tsiku langa lopatulika,+ sabatalo mukalitcha tsiku losangalatsa kwambiri, tsiku lopatulika ndi lolemekezeka la Yehova,+ ndipo mukalilemekeza m’malo moyenda njira zanu, m’malo mopeza zinthu zosangalatsa inuyo, ndiponso m’malo molankhula zopanda pake, 14 pamenepo mudzasangalala kwambiri mwa Yehova.+ Ine ndidzakuchititsani kuti mukwere m’malo okwezeka a dziko lapansi,+ ndipo ndidzakuchititsani kuti mudye zochokera m’cholowa cha Yakobo kholo lanu,+ pakuti pakamwa pa Yehova panena zimenezi.”+
59 Dzanja la Yehova silinafupike moti n’kulephera kupulumutsa,+ komanso khutu lake silinagonthe moti n’kulephera kumva.+ 2 Ayi si choncho. Koma zolakwa za anthu inu n’zimene zakulekanitsani ndi Mulungu wanu,+ ndipo machimo anu amuchititsa kuti akubisireni nkhope yake, kuti asamve zimene mukunena.+ 3 Pakuti m’manja mwanu mwaipitsidwa ndi magazi,+ ndipo zala zanu zaipitsidwa ndi zolakwa.+ Milomo yanu yanena zabodza. Lilime lanu limangokhalira kunena zinthu zopanda chilungamo.+ 4 Palibe amene akufuula mwachilungamo,+ ndipo palibe amene amalankhula mokhulupirika akapita kukhoti. Anthu inu mukukhulupirira zinthu zachabechabe+ ndipo mukulankhula zopanda pake.+ Mwatenga pakati pa mavuto ndipo mwabereka zopweteka.+
5 Iwo aikira mazira a njoka yapoizoni, ndipo ankangokhalira kuluka ukonde wa kangaude.+ Aliyense wodya mazira a njoka yapoizoniyo amafa, ndipo dzira limene laswedwa limaswa mphiri.+ 6 Ukonde wawo wa kangaude sudzakhala chovala chawo, ndipo iwo sadzavala zochita zawo.+ Ntchito zawo n’zopweteka ena, ndipo m’manja mwawo muli ntchito zachiwawa.+ 7 Mapazi awo amangothamangira kukachita zoipa,+ ndipo amafulumira kuti akakhetse magazi osalakwa.+ Maganizo awo ndi opweteka anzawo.+ M’misewu mwawo amangokhalira kusakazana ndi kuwonongana.+ 8 Iwo amangonyalanyaza njira yamtendere,+ ndipo m’njira zawo mulibe chilungamo.+ Misewu yawo aikhotetsakhotetsa.+ Palibe munthu aliyense woyenda mmenemo amene adzadziwe mtendere.+
9 N’chifukwa chake chilungamo chatitalikira kwambiri, ndipo zolungama sizikutipeza. Tinali kuyembekezera kuunika koma m’malomwake tikungoona mdima. Tinali kuyembekezera kuwala koma tikungoyendabe mu mdima wosatha.+ 10 Tikungoyenda ndi khoma ngati anthu akhungu, ndipo tikungofufuzafufuza ngati anthu opanda maso.+ Tapunthwa masanasana ngati kuti tili mu mdima wamadzulo. Pakati pa anthu ojintcha, tikungokhala ngati anthu akufa.+ 11 Tonsefe tikungolira ngati zimbalangondo ndipo tikungokhalira kubuula momvetsa chisoni ngati njiwa.+ Tinali kuyembekezera chilungamo+ koma sichinabwere. Tinali kuyembekezera chipulumutso koma chakhala nafe kutali.+ 12 Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso panu,+ ndipo tchimo lathu lililonse likupereka umboni wotsutsana nafe.+ Pakuti zolakwa zathu zili pa ife, ndipo zochimwa zathu tikuzidziwa bwino.+ 13 Ife taphwanya malamulo ndipo tamukana Yehova.+ Tabwerera m’mbuyo n’kumusiya Mulungu wathu. Tanena zinthu zopondereza ena ndi zopanduka.+ Taganiza mawu achinyengo mumtima mwathu n’kumawalankhula chapansipansi.+ 14 Chilungamo tinachikankhira m’mbuyo,+ ndipo chilungamocho chinakangoima patali.+ Pakuti choonadi chapunthwa ngakhale m’bwalo la mumzinda, ndipo zinthu zolungama zikulephera kulowamo.+ 15 Choonadi chikusowa+ ndipo aliyense wokana zoipa akusakazidwa.+
Yehova anaona zimenezi ndipo zinamuipira m’maso mwake poona kuti panalibe chilungamo.+ 16 Iye ataona kuti panalibe munthu aliyense woti n’kuthandizapo, anadabwa kwambiri poona kuti palibe amene akulowererapo.+ Chotero anapulumutsa anthu ndi dzanja lake, ndipo chilungamo chake n’chimene chinamulimbikitsa kuchita zimenezo.+ 17 Choncho iye anavala chilungamo monga chovala chodzitetezera chamamba achitsulo,+ ndiponso anavala chisoti cholimba chachipulumutso kumutu kwake.+ Kuwonjezera apo, anavala chilungamo monga chovala kuti akapereke chilango kwa adani ake+ ndiponso kuchita zinthu modzipereka kwambiri kunali ngati chovala chake chodula manja.+ 18 Iye adzawapatsa mphoto mogwirizana ndi zochita zawo.+ Adani ake adzawapatsa mkwiyo ndipo anthu otsutsana naye adzawapatsa chilango chowayenerera.+ Zilumbanso adzazipatsa chilango choyenerera.+ 19 Amene ali kolowera dzuwa adzayamba kuopa dzina la Yehova,+ ndipo amene ali kotulukira dzuwa adzaopa ulemerero wake.+ Pakuti iye adzabwera ngati mtsinje woyambitsa mavuto woyendetsedwa ndi mzimu wa Yehova.+
20 “Wowombolayo+ adzabwera ku Ziyoni+ ndiponso kwa mbadwa za Yakobo zimene zasiya zolakwa zawo,”+ akutero Yehova.
21 Yehova wanena kuti: “Koma pangano langa ndi iwowo+ ndi ili:
“Mzimu wanga umene uli pa iwe+ ndi mawu anga amene ndaika m’kamwa mwako,+ sizidzachoka m’kamwa mwako ndiponso m’kamwa mwa ana ako kapenanso m’kamwa mwa ana a ana ako, kuyambira panopa mpaka kalekale,” watero Yehova.+
60 “Imirira+ mkazi iwe! Onetsa kuwala kwako,+ pakuti kuwala kwako kwafika,+ ndipo ulemerero wa Yehova wakuunika.+ 2 Taona! Mdima+ udzaphimba dziko lapansi, ndipo mdima wandiweyani udzaphimba mitundu ya anthu. Koma kuwala kwa Yehova kudzafika pa iwe, ndipo ulemerero wake udzaonekera pa iwe.+ 3 Mitundu ya anthu idzatsata kuwala kwako,+ ndipo mafumu+ adzatsata kunyezimira kwako.+
4 “Takweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse asonkhanitsidwa pamodzi.+ Abwera kwa iwe.+ Kuchokera kutali, ana ako aamuna akubwera limodzi ndi ana ako aakazi, amene adzasamalidwe atanyamulidwa m’manja.+ 5 Pa nthawi imeneyo, nkhope yako idzasangalala ukadzaona zimenezi.+ Mtima wako udzanthunthumira ndi kufutukuka, chifukwa chuma cha m’nyanja chidzabwera kwa iwe. Katundu wa mitundu ya anthu adzabwera kwa iwe.+ 6 Chikhamu cha ngamila zamphongo zing’onozing’ono za ku Midiyani ndi ku Efa+ chidzadzaza dziko lako. Anthu onse a ku Sheba+ adzabwera atanyamula golide ndi lubani. Iwo adzatamanda Yehova pamaso pa anthu onse.+ 7 Nkhosa zonse za ku Kedara+ zidzasonkhanitsidwa kwa iwe. Nkhosa zamphongo za ku Nebayoti+ zidzakutumikira.+ Ine ndidzazilandira paguwa langa lansembe,+ ndipo ndidzakongoletsa nyumba yanga yokongola.+
8 “Kodi amene akubwera chouluka ngati mtambowa ndani?+ Ndani awa akubwera ngati nkhunda zimene zikuulukira kumakomo a makola awo? 9 Pakuti zilumba zidzayembekezera ine.+ Nazonso zombo za ku Tarisi+ zidzayembekezera ine ngati poyamba paja, kuti zikubweretsere ana ako aamuna kuchokera kutali.+ Iwo adzabwera atanyamula siliva ndi golide wawo,+ kuti alemekeze dzina+ la Yehova Mulungu wako ndi Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakhala atakukongoletsa.+ 10 Alendo adzamanga mipanda yako,+ ndipo mafumu awo adzakutumikira.+ Ine ndinakulanga mu mkwiyo wanga,+ koma chifukwa cha kukoma mtima kwanga ndidzakuchitira chifundo.+
11 “Zipata zako zidzakhala zotsegula nthawi zonse.+ Sizidzatsekedwa usana ndi usiku kuti chuma cha mitundu ya anthu chibwere kwa iwe,+ ndipo mafumu awo ndiwo adzakhale patsogolo pochita zimenezi.+ 12 Pakuti mtundu uliwonse ndi ufumu uliwonse umene sudzakutumikira udzawonongedwa, ndipo mitundu ya anthu idzasakazidwa ndithu.+
13 “Ulemerero wa Lebanoni udzabwera kwa iwe. Mtengo wofanana ndi mkungudza, mtengo wa ashi, ndiponso mtengo wa paini zidzabwera pa nthawi imodzi,+ kuti zikongoletse malo anga opatulika,+ ndipo ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.+
14 “Ana a anthu okusautsa adzabwera kwa iwe atawerama.+ Onse amene anali kukuchitira chipongwe adzagwada pamapazi ako,+ ndipo adzakutcha mzinda wa Yehova, Ziyoni+ wa Woyera wa Isiraeli.
15 “M’malo mokhala wosiyidwa mpaka kalekale ndi wodedwa, popanda aliyense wodutsa mwa iwe,+ ine ndidzakuika monga chinthu chonyaditsa mpaka kalekale, ndiponso chinthu chokondweretsa ku mibadwomibadwo.+ 16 Iwe udzayamwa mkaka wa mitundu ya anthu,+ ndipo udzayamwa bere la mafumu.+ Udzadziwadi kuti ine Yehova+ ndine Mpulumutsi wako,+ ndipo Wamphamvu+ wa Yakobo ndiye Wokuwombola.+ 17 M’malo mwa mkuwa, ndidzabweretsa golide.+ M’malo mwa chitsulo, ndidzabweretsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweretsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweretsa chitsulo. Ndidzaika mtendere kuti ukhale ngati wokuyang’anira,+ ndi chilungamo kuti chikhale ngati wokupatsa ntchito.+
18 “M’dziko lako simudzamvekanso zachiwawa. Mkati mwa malire ako simudzakhalanso kusakaza kapena kuwononga.+ Mipanda yako udzaitcha Chipulumutso+ ndipo zipata zako udzazitcha Chitamando. 19 Dzuwa silidzakhalanso lokuunikira masana, ndipo mwezi sudzakuunikiranso. Kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale,+ ndipo Mulungu wako adzakhala kukongola kwako.+ 20 Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzapitanso kumdima. Pakuti kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale,+ ndipo masiku ako olira adzakhala atatha.+ 21 Anthu ako onse adzakhala olungama.+ Iwo adzakhala m’dzikomo mpaka kalekale.+ Anthuwo adzakhala mmera wobzalidwa ndi ine+ ndiponso ntchito ya manja anga,+ kuti ineyo ndikongoletsedwe.+ 22 Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.+ Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.”+
61 Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+ pakuti Yehova wandidzoza+ kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+ Wandituma kuti ndikamange zilonda za anthu osweka mtima,+ ndikalengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndiponso ndikatsegule maso a akaidi.+ 2 Wandituma kuti ndikalengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima,+ ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu.+ Wanditumanso kuti ndikatonthoze anthu onse olira,+ 3 ndiponso kuti anthu onse amene akulirira Ziyoni ndiwapatse nsalu yovala kumutu m’malo mwa phulusa,+ ndiwapatse mafuta kuti azisangalala+ m’malo molira, ndiwapatse chovala choti azivala ponditamanda m’malo mokhala otaya mtima.+ Iwo adzatchedwa mitengo ikuluikulu ya chilungamo,+ yobzalidwa ndi Yehova+ kuti iyeyo akongole.+ 4 Iwo adzamanganso malo amene akhala owonongeka kwa nthawi yaitali.+ Adzamanga malo amene anasakazidwa kalekale.+ Adzakonzanso mizinda yowonongedwa,+ malo amene akhala osakazidwa ku mibadwomibadwo.
5 “Alendo adzabwera n’kumaweta ziweto zanu.+ Anthu ochokera kwina+ adzakhala olima minda yanu ndi osamalira minda yanu ya mpesa.+ 6 Inuyo mudzatchedwa ansembe a Yehova.+ Anthu adzakutchani atumiki+ a Mulungu wathu.+ Mudzadya zinthu zochokera ku mitundu ya anthu+ ndiponso mudzalankhula za inuyo mokondwera, chifukwa cha chuma ndi ulemerero zimene mudzapeze kwa mitunduyo.+ 7 M’malo mwa manyazi, mudzalandira zinthu zochuluka kuwirikiza kawiri,+ ndipo m’malo mochita manyazi, anthu anga adzafuula ndi chisangalalo chifukwa cha gawo lawo.+ Iwo adzakhala ndi gawo lowirikiza kawiri m’dziko lawo,+ ndipo adzasangalala mpaka kalekale.+ 8 Pakuti ine Yehova ndimakonda chilungamo.+ Ndimadana ndi zauchifwamba ndi kupanda chilungamo.+ Ndidzawapatsa malipiro awo mokhulupirika,+ ndipo ndidzachita nawo pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale.+ 9 Ana awo adzadziwika pakati pa mitundu ya anthu,+ ndipo mbadwa zawo zidzadziwika pakati pa anthu osiyanasiyana. Onse owaona adzazindikira+ kuti iwo ndi ana odalitsidwa ndi Yehova.”+
10 Ndithu ine ndidzakondwera mwa Yehova.+ Moyo wanga udzasangalala ndi Mulungu wanga.+ Pakuti iye wandiveka zovala zachipulumutso.+ Wandiveka malaya akunja achilungamo odula manja,+ ngati mkwati amene wavala chovala chakumutu mofanana ndi wansembe,+ ndiponso ngati mkwatibwi amene wavala zinthu zake zodzikongoletsera.+ 11 Pakuti monga momwe dziko lapansi limatulutsira zomera zake, ndiponso monga momwe munda umameretsera zinthu zimene zabzalidwa mmenemo,+ momwemonso Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzameretsa chilungamo+ ndi chitamando pamaso pa mitundu yonse.+
62 Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala phee,+ ndipo chifukwa cha Yerusalemu+ sindidzakhala chete mpaka kulungama kwake kutakhala ngati kuwala,+ ndiponso mpaka chipulumutso chake chitakhala ngati muuni woyaka moto.+
2 “Mitundu ya anthu idzaona kulungama kwako+ mkazi iwe,+ ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.+ Iwe udzatchedwa ndi dzina latsopano+ limene pakamwa pa Yehova padzasankhe. 3 Udzakhala chisoti chokongola m’dzanja la Yehova,+ ndiponso chisoti chachifumu m’dzanja la Mulungu wako. 4 Sudzatchedwanso mkazi wosiyidwa mpaka kalekale+ ndipo dziko lako silidzatchedwanso labwinja.+ Koma iweyo dzina lako lidzakhala “Ndimakondwera Naye,”+ ndipo dziko lako lidzatchedwa “Mkazi Wokwatiwa.” Pakuti Yehova adzakondwera nawe ndipo dziko lako lidzakhala ngati mkazi wokwatiwa.+ 5 Pakuti monga momwe mnyamata amatengera namwali kuti akhale mkazi wake, ana ako aamuna adzakutenga kuti ukhale mkazi wawo.+ Monga momwe mkwati amakhalira wachimwemwe chifukwa cha mkwatibwi,+ Mulungu wako adzakhala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe.+ 6 Iwe Yerusalemu, ine ndaika alonda pamakoma a mpanda wako.+ Nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu ndi usiku wonse wathunthu, iwo asakhale chete.+
“Inu amene mukutchula dzina la Yehova,+ musakhale chete.+ 7 Musaleke kumukumbutsa mpaka atakhazikitsa Yerusalemu monga chinthu chofunika kutamandidwa padziko lapansi.”+
8 Yehova walumbira ndi dzanja lake lamanja+ ndiponso ndi mkono wake wamphamvu+ kuti: “Sindidzaperekanso mbewu zanu kwa adani anu ngati chakudya,+ ndipo alendo sadzamwanso vinyo wanu watsopano+ amene munachita kumuvutikira. 9 Koma anthu amene anakolola mbewuzo ndi amene adzazidye, ndipo adzatamanda Yehova. Amene anasonkhanitsa vinyoyo ndi amene adzamumwe m’mabwalo anga oyera.”+
10 Tulukani! Tulukani pazipata anthu inu. Lambulani njira yodutsa anthu.+ Konzani msewu. Ukonzeni ndithu. Chotsanimo miyala.+ Akwezereni chizindikiro anthu a mitundu yosiyanasiyana.+
11 Taonani! Yehova wachititsa kuti mawu awa amveke mpaka kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi:+ “Anthu inu, uzani mwana wamkazi wa Ziyoni+ kuti, ‘Taona! Chipulumutso chako chikubwera.+ Taona! Mphoto imene iye akufuna kupereka ili ndi iyeyo,+ ndipo malipiro amene akufuna kupereka ali pamaso pake.’”+
12 Iwo adzatchedwa anthu oyera,+ owomboledwa ndi Yehova.+ Iweyo udzatchedwa “Mzinda Umene Anaufunafuna,” “Mzinda Umene Sanausiyiretu.”+
63 Kodi amene akuchokera ku Edomuyu+ ndi ndani, amene akuchokera ku Bozira+ atavala zovala zowala zamitundumitundu, amene zovala zake ndi zolemekezeka, ndiponso amene akuyenda mwamphamvu chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake?
“Ndi ine, amene ndimalankhula mwachilungamo,+ amene ndili ndi mphamvu zambiri zopulumutsa.”+
2 N’chifukwa chiyani zovala zanu zili zofiira, ndipo n’chifukwa chiyani zovala zimene mwavala zikuoneka ngati za munthu woponda mphesa m’choponderamo mphesa?+
3 “Moponderamo mphesa ndapondapondamo ndekha,+ chifukwa palibe munthu amene anali nane wochokera pakati pa mitundu ya anthu. Iwo ndawapondaponda mu mkwiyo wanga,+ ndipo ndawapondereza mu ukali wanga.+ Magazi awo awazikira pazovala zanga,+ ndipo ndaipitsa zovala zanga zonse. 4 Pakuti tsiku lobwezera lili mumtima mwanga,+ ndipo chaka choti anthu anga awomboledwe chafika. 5 Ndinayang’anayang’ana, koma panalibe wondithandiza. Ndinayamba kudabwa, koma panalibe woti angandichirikize.+ Choncho ndinabweretsa chipulumutso ndi dzanja langa,+ ndipo ukali wanga+ ndi umene unandichirikiza. 6 Ndinapondaponda mitundu ya anthu mu mkwiyo wanga, ndipo ndinawaledzeretsa ndi ukali wanga.+ Ndinachititsa kuti magazi awo atuluke mwamphamvu n’kutayikira pansi.”+
7 Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+ Ndidzatamanda Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehova watichitira.+ Ndidzauza nyumba ya Isiraeli zabwino zochuluka+ zimene iye wawachitira chifukwa cha chifundo chake,+ komanso chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha ndiponso kwakukulu. 8 Iye anati: “Ndithu awa ndi anthu anga,+ ana amene sadzachita zachinyengo.”+ Choncho iye anakhala Mpulumutsi wawo.+ 9 Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.+ Mthenga amene iye anawatumizira, anawapulumutsa.+ Chifukwa cha chikondi chake ndi chisoni chake, iye anawawombola.+ Anawakweza m’mwamba ndi kuwanyamula masiku onse akale.+
10 Koma iwo anapanduka+ ndi kukhumudwitsa mzimu wake woyera.+ Chotero iye anasintha n’kukhala mdani+ wawo ndipo anachita nawo nkhondo.+ 11 Iwo anayamba kukumbukira masiku akale, masiku a Mose mtumiki wake, ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa m’nyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake uja, ali kuti?+ Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+ 12 Ali kuti amene anachititsa mkono wake wokongola+ kupita kudzanja lamanja la Mose, amene anagawanitsa madzi pamaso pawo+ kuti adzipangire dzina lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+ 13 amene anawawolotsa pamadzi amphamvu moti sanapunthwe, mofanana ndi hatchi m’chipululu?+ 14 Monga momwe chilombo chakutchire chimatsetserekera kuchigwa, mzimu wa Yehova unawapumitsa.”+
Chotero inu munatsogolera anthu anu kuti mudzipangire dzina lokongola.+
15 Yang’anani muli kumwamba,+ ndipo muone kuchokera pamalo anu okhala apamwamba, oyera ndi okongola.+ Kodi mtima wanu wodzipereka kwambiri+ ndiponso mphamvu zanu zonse zili kuti? Kodi kubwadamuka kwa m’mimba mwanu+ ndi chifundo+ chanu zili kuti? Inuyo mwaleka kundichitira zimenezi.+ 16 Inutu ndinu Atate wathu.+ Ngakhale kuti Abulahamu sanatidziwe ndipo Isiraeli sanatizindikire, inuyo Yehova ndinu Atate wathu. Dzina lanu ndinu Wotiwombola wakalekale.+ 17 N’chifukwa chiyani inu Yehova mukutichititsa kuchoka panjira zanu? N’chifukwa chiyani mukuumitsa mtima wathu kuti tisakuopeni?+ Bwererani chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.+ 18 Kwa kanthawi kochepa, anthu anu oyera+ anali ndi zinthu. Koma adani athu apondaponda malo anu opatulika.+ 19 Kwanthawi yaitali, takhala ngati anthu amene simunawalamulirepo, ngati anthu amene sanatchedwepo ndi dzina lanu.+
64 Zikanakhalatu bwino mukanang’amba kumwamba, mukanatsika pansi pano,+ komanso mapiri akanagwedezeka chifukwa cha inu,+ 2 ngati momwe zimakhalira moto ukayatsa tchire la zitsamba ndiponso ukawiritsa madzi. Zikanakhala bwino mukanachita zimenezi kuti dzina lanu lidziwike kwa adani anu,+ ndiponso kuti mitundu ya anthu igwedezeke chifukwa cha inu.+ 3 Inu munatsikira pansi pano pamene munachita zinthu zochititsa mantha+ zimene sitinali kuyembekezera. Mapiri anagwedezeka chifukwa cha inu.+ 4 Kuyambira kalekale palibe amene anamvapo+ kapena kuganizira za Mulungu wina kupatula inu,+ ndipo palibe amene anamuonapo. Inu mumathandiza munthu amene akukuyembekezerani.+ 5 Mwabwera kudzathandiza anthu amene akukondwera ndiponso amene akuchita zolungama,+ anthu amene amakukumbukirani potsatira njira zanu.+
Koma inuyo munakwiya+ chifukwa chakuti ifeyo tinkangopitirizabe kuchimwa+ kwanthawi yaitali. Choncho kodi ndife oyenera kupulumutsidwa?+ 6 Tonsefe takhala ngati munthu wodetsedwa, ndipo zochita zathu zonse zolungama zili ngati kansalu kamene mkazi amavala pa nthawi yosamba.+ Tonsefe tidzayoyoka ngati masamba+ ndipo zolakwa zathu zidzatiuluzira kutali ngati mphepo.+ 7 Palibe amene akutamanda dzina lanu.+ Palibe amene akutekeseka kuti akufunefuneni ndi kukugwirani mwamphamvu, pakuti mwatibisira nkhope yanu+ ndipo mwatichititsa kuti tisungunuke+ ndi mphamvu ya zolakwa zathu.
8 Komatu inu Yehova, inu ndinu Atate wathu.+ Ife ndife dongo+ ndipo inu ndinu Wotiumba.+ Tonsefe ndife ntchito ya manja anu.+ 9 Inu Yehova musatikwiyire kwambiri,+ ndipo musakumbukire zolakwa zathu kwamuyaya.+ Chonde, kumbukirani kuti tonsefe ndife anthu anu.+ 10 Mizinda yanu yoyera+ yasanduka chipululu. Ziyoni+ wangosanduka chipululu basi, ndipo Yerusalemu wasanduka bwinja.+ 11 Nyumba yathu yoyera ndiponso yokongola+ imene makolo athu anali kukutamandiranimo,+ yasanduka chinthu chofunika kuchitentha pamoto,+ ndipo zinthu zathu zonse zabwinozabwino+ zasakazidwa. 12 Poona zinthu zonsezi, kodi mupitiriza kumangokhala osachitapo kanthu,+ inu Yehova? Kodi muzingoonerera pamene ife tikusautsidwa koopsa?+
65 “Ine ndalola kuti anthu amene sanafunse za ine+ andifunefune.+ Ndalola kuti anthu amene sanandifunefune andipeze.+ Ndanena kuti, ‘Ndili pano, ndili pano!’+ kwa mtundu umene sunaitane pa dzina langa.+
2 “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,*+ amene akuyenda m’njira yoipa+ potsatira maganizo awo,+ 3 anthu amene akundichitira mwano+ nthawi zonse m’maso muli gwa! Amene amapereka nsembe m’minda,+ amene amafukiza nsembe zautsi+ panjerwa, 4 amene amakhala pansi kumanda,+ amene amakhala usiku wonse m’tinyumba ta alonda, amene amadya nyama ya nkhumba,+ ndipo m’miphika mwawo muli msuzi wa zinthu zodetsedwa.+ 5 Iwo amanena kuti, ‘Khala pawekha. Usandiyandikire, kuti ndingakupatsire chiyero changa.’+ Iwo ali ngati utsi m’mphuno mwanga,+ ngati moto woyaka tsiku lonse.+
6 “Taonani! Zalembedwa pamaso panga.+ Ine sindidzakhala chete,+ koma ndidzapereka mphoto.+ Mphotoyo ndidzaiika pachifuwa pawo,+ 7 chifukwa cha zolakwa zawo ndi zolakwa za makolo awo pa nthawi imodzi,”+ watero Yehova. “Popeza afukiza nsembe zautsi pamapiri ndipo andinyoza+ pazitunda,+ ine ndidzawayezera mphoto yawo choyamba, n’kuiika pachifuwa pawo.”+
8 Yehova wanena kuti: “Monga momwe vinyo watsopano+ amapezekera m’tsango la mphesa ndipo wina amanena kuti, ‘Musaliwononge,+ pakuti muli dalitso mmenemu,’+ inenso ndidzachita zomwezo chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawawononge onse.+ 9 Mwa Yakobo ndidzatulutsamo mwana,+ ndipo mwa Yuda ndidzatulutsamo yemwe adzalandire cholowa cha mapiri anga.+ Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapatsidwa dziko lamapirilo,+ ndipo atumiki anga adzakhala mmenemo.+ 10 Sharoni+ adzakhala malo odyetserapo nkhosa.+ Chigwa cha Akori+ chidzakhala malo opumulirapo ng’ombe za anthu anga amene andifunafuna.+
11 “Koma anthu inu mwamusiya Yehova.+ Mwaiwala phiri langa loyera.+ Inu mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi.+ Mumadzaza chikho ndi vinyo wosakaniza n’kupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.+ 12 Choncho ine ndidzakonzeratu zoti anthu inu mudzaphedwe ndi lupanga.+ Nonsenu mudzawerama kuti akupheni,+ popeza ndinakuitanani+ koma simunayankhe. Ndinalankhula koma simunamvere.+ Munapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga+ ndipo munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”+
13 Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Atumiki anga adzadya,+ koma inuyo mudzakhala ndi njala.+ Atumiki anga adzamwa,+ koma inuyo mudzakhala ndi ludzu.+ Atumiki anga adzasangalala,+ koma inuyo mudzachita manyazi.+ 14 Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima,+ koma inuyo mudzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo mudzafuula chifukwa chosweka mtima.+ 15 Anthu inu mudzasiya dzina lanu kuti anthu anga osankhidwa mwapadera aziligwiritsa ntchito potemberera ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzakuphani mmodzi ndi mmodzi,+ koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.+ 16 Chotero aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi adzadalitsidwa ndi Mulungu wokhulupirika.+ Aliyense wolumbira padziko lapansi adzalumbira pa Mulungu wokhulupirika,+ chifukwa masautso akale adzaiwalika ndipo sadzaonedwanso ndi maso anga.+
17 “Pakuti ndikulenga kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano.+ Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso+ ndipo sizidzabweranso mumtima.+ 18 Koma kondwerani anthu inu,+ ndipo sangalalani kwamuyaya ndi zimene ndikulenga.+ Pakuti ndikulenga Yerusalemu kuti akhale chinthu chosangalatsa ndipo anthu ake akhale chinthu chokondweretsa.+ 19 Ndidzasangalala ndi Yerusalemu ndipo ndidzakondwera ndi anthu anga.+ Mwa iye simudzamvekanso kulira kokweza mawu kapena kulira kwachisoni.”+
20 “Kumeneko sikudzakhalanso mwana woyamwa wongokhala ndi moyo masiku ochepa okha,+ kapena nkhalamba imene sidzakwanitsa masiku ake.+ Pakuti ngakhale munthu womwalira ali ndi zaka 100 adzaoneka ngati kamnyamata, ndipo wochimwa, ngakhale ali ndi zaka 100, temberero lidzamugwera.+ 21 Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo.+ Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+ 22 Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo,+ ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.+ 23 Sadzagwira ntchito pachabe+ komanso sadzaberekera tsoka,+ chifukwa iwo ndiponso ana awo+ ndi odalitsidwa ndi Yehova.+ 24 Iwo asanandiitane, ine ndidzayankha.+ Asanamalize kulankhula, ine ndidzamva.+
25 “Mmbulu+ ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi.+ Mkango udzadya udzu ngati ng’ombe yamphongo,+ ndipo njoka izidzadya fumbi.+ Zimenezi sizidzapweteka aliyense+ kapena kuwononga chilichonse m’phiri langa lonse loyera,”+ watero Yehova.
66 Yehova wanena kuti: “Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu,+ ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.+ Kodi anthu inu mungandimangire nyumba yotani?+ Ndipo malo oti ine ndingapumulirepo, ali kuti?”+
2 “Zinthu zonsezi ndinazipanga ndi dzanja langa, choncho zinakhalapo,”+ akutero Yehova. “Ine ndidzayang’ana munthu amene ali wosautsidwa, wosweka mtima,+ ndiponso wonjenjemera ndi mawu anga.+
3 “Munthu amene akupha ng’ombe yamphongo ali ngati wopha munthu.+ Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati wothyola khosi la galu.+ Wopereka mphatso ali ngati wopereka magazi a nkhumba.+ Wopereka lubani wachikumbutso+ ali ngati wopereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga.+ Anthuwo asankha njira zawozawo, ndipo amasangalala ndi zinthu zawo zonyansa.+ 4 Ineyo ndidzasankha njira zowazunzira.+ Ndidzawabweretsera zinthu zimene amachita nazo mantha+ chifukwa ndinaitana koma palibe amene anayankha. Ndinalankhula koma palibe amene anamvera.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga ndipo anasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”+
5 Inu amene mukunjenjemera ndi mawu ake, imvani mawu a Yehova:+ “Abale anu amene akudana nanu,+ amene akukusalani chifukwa cha dzina langa,+ anati, ‘Alemekezeke Yehova!’+ Mulungu adzaonekera ndipo inu mudzasangalala,+ koma iwowo ndi amene adzachite manyazi.”+
6 Mumzinda mukumveka phokoso lachisokonezo, phokoso lochokera kukachisi.+ Limeneli ndi phokoso losonyeza kuti Yehova akubwezera adani ake chilango chowayenerera.+
7 Mkazi anabereka asanayambe kumva zowawa za pobereka.+ Ululu wa pobereka usanamubwerere, iye anabereka mwana wamwamuna.+ 8 Ndani anamvapo zinthu ngati zimenezi?+ Ndani anaonapo zinthu zoterezi?+ Kodi dziko+ limatulutsidwa ndi zowawa za pobereka tsiku limodzi lokha?+ Kapena kodi mtundu+ umabadwa nthawi imodzi?+ Pakuti Ziyoni wamva zowawa za pobereka ndipo wabereka ana ake aamuna.
9 “Kodi ine ndingachititse kuti chiberekero chitseguke koma osachititsa kuti mwana abadwe?”+ akutero Yehova. “Kapena kodi ndingachititse kuti mwana atsale pang’ono kubadwa kenako n’kutseka chiberekero?” watero Mulungu wanu.
10 Sangalalani ndi Yerusalemu ndipo kondwerani naye,+ inu nonse omukonda.+ Kondwerani naye kwambiri, inu nonse amene mukumulirira,+ 11 chifukwa mudzayamwa bere lake ndipo mudzakhuta kutonthoza kwake. Komanso mudzayamwa mkaka wake ndipo mudzasangalala kwambiri ndi bere lake laulemerero.+ 12 Pakuti Yehova wanena kuti: “Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje+ ndi ulemerero wa mitundu ya anthu ngati mtsinje wosefukira,+ ndipo inu mudzayamwadi.+ Adzakunyamulani m’manja ndipo adzakusisitani mwachikondi atakuikani pamwendo.+ 13 Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu,+ ndipo mudzatonthozedwa chifukwa cha Yerusalemu.+ 14 Mudzaona zimenezi ndipo mtima wanu udzasangalala.+ Mafupa anu+ adzakhala ndi mphamvu ngati udzu wobiriwira.+ Dzanja la Yehova lidzadziwika kwa atumiki ake,+ koma iye adzakwiyira adani ake.”+
15 “Pakuti Yehova akubwera ngati moto,+ ndipo magaleta ake ali ngati mphepo yamkuntho+ kuti adzawabwezere mwaukali ndi mokwiya, ndiponso kuti adzawadzudzule ndi malawi a moto.+ 16 Pakuti ngati moto woyaka, Yehova adzaweruza anthu onse ndi lupanga lake,+ ndipo anthu ophedwa ndi Yehova adzakhala ambiri.+ 17 Anthu amene akudzipatula ndi kudziyeretsa kuti apite kuminda+ n’kukaima kuseri kwa fano limene lili pakati pa mundawo, amene akudya nyama ya nkhumba+ ndi chinthu chonyansa, amene akudya ngakhale makoswe,+ onsewo adzathera limodzi,” akutero Yehova. 18 “Popeza ndikudziwa ntchito zawo+ ndi maganizo awo,+ ine ndikubwera kudzasonkhanitsa pamodzi mitundu yonse ndi zilankhulo zonse za anthu,+ ndipo iwo adzabwera n’kuona ulemerero wanga.”+
19 “Ndidzachita zinthu zazikulu pakati pawo monga chizindikiro.+ Opulumuka ena ndidzawatumiza ku mitundu ya anthu,+ ku Tarisi,+ ku Puli, ndi ku Ludi.+ Ndidzawatumiza kwa anthu odziwa kukoka uta ku Tubala ndi ku Yavani.+ Ndidzawatumiza kuzilumba zakutali,+ kwa anthu amene sanamve mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga.+ Iwo adzanenadi za ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu.+ 20 Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse+ monga mphatso kwa Yehova.+ Adzayenda pamahatchi, pangolo, pangolo zotseka pamwamba, panyulu,* ndi pangamila zazikazi zothamanga,+ popita kuphiri langa loyera,+ ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene ana a Isiraeli amabweretsera mphatso m’nyumba ya Yehova, ataiika m’chiwiya choyera,”+ watero Yehova.
21 “Pakati pawo ndidzatengapo anthu ena kuti akhale ansembe ndi Alevi,” watero Yehova.
22 “Pakuti monga momwe kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano+ zimene ndikupanga zidzakhalirebe pamaso panga,+ momwemonso ana anu+ ndi dzina lanu zidzakhalapo mpaka kalekale,”+ akutero Yehova.
23 “Kuyambira mwezi watsopano mpaka mwezi wina watsopano, ndiponso sabata ndi sabata, anthu onse adzabwera kudzagwada pamaso panga,”+ watero Yehova. 24 “Iwo adzapita kukaona mitembo ya anthu amene anali kuphwanya malamulo anga,+ pakuti mphutsi zodya mitemboyo sizidzafa. Moto woinyeketsa sudzazima+ ndipo idzakhala chinthu chonyansa kwa anthu onse.”+
Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
Zimenezi ndi zonyansa zotsalira poyenga zitsulo.
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
Ena amati “akasusum’njira.”
Ena amati “masikiyo.”
Mawu ake enieni, “nyumba zimene mumakhala moyo.”
“Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.
Ena amati “saka.”
Chimenechi ndi chizindikiro chimene anali kuchiika pathupi la kapolo kapena mkaidi.
Zikuoneka kuti amenewa anali malo aakulu pafupifupi mahekitala anayi.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
Muyezo umodzi wa efa ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
Onani Zakumapeto 5.
Ena amati “zonzuna.”
Dzinali limatanthauza kuti, “Otsala Ochepa (kapena, Otsala) Adzabwerera.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Dzinali limatanthauza kuti, “Fulumira Iwe Zofunkha, kapena Kufulumirira Zofunkha. Iye Wabwera Mofulumira ku Zolanda.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “mlulu.”
Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”
Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”
Onani mawu a m’munsi pa vesi 16.
Onani mawu a m’munsi pa vesi 16.
“Otsala ochepa adzabwerera.” M’Chiheberi mawu amenewa n’chimodzimodzi ndi dzina lakuti “Seari-yasubu” limene lili pa 7:3. Onani mawu a m’munsi pamenepo.
Ena amati “nyalugwe.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Zimenezi zikuimira ziwanda kapena nyama zenizeni zimene anthu akaziona ankayamba kuganiza za ziwanda.
“Nungu” ndi nyama yam’tchire yomwe ili ndi minga zodzitetezera thupi lonse.
Ena amati “chipserero.”
Kapena kuti “tsindwi.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Mawu ake enieni, “Pomatha zaka zitatu, malinga ndi zaka za munthu waganyu.” Nthawi imene munthu waganyu anali kugwira ntchito sanali kuiwonjezera kapena kuichepetsa. Chotero, izi zikutanthauza kuti nthawi ya kutha kwa ulemerero wa Mowabu inali yosasinthika.
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa kumbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “mlulu.”
“Fulakesi” ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Kapena kuti “mkulu wa asilikali.”
Kapena kuti “atavala zovala zam’kati zokha.”
Mawu akuti “chipululu cha nyanja” mwina akutanthauza chigawo cha kum’mwera cha dziko lakale la Babulo, kumene mitsinje ya Firate ndi Tigirisi inali kusefukira chaka chilichonse.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “malinga ndi zaka za munthu waganyu.” Onani mawu a m’munsi pa Yes 16:14.
Mwina kutanthauza chigawo cha kum’mawa kapena kudera lakutali.
Kapena, “vinyo yemwe nsenga zake zadikha pansi chifukwa chokhalitsa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Kapena kuti “ng’ona.” Mwina imeneyi inali ng’ona kapena chilombo cham’nyanja.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Pa Chiheberi vesi limeneli lili ngati kandakatulo kobwerezabwereza, kokhala ngati kanyimbo ka ana.
Chimenechi chinali chipangizo chimene anali kuchigwiritsa ntchito pofuna kuonetsetsa kuti pamalo pakhale pa fulati.
Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “mbewu zinanso” akutanthauza mtundu wa tirigu wosakoma kwenikweni umene unali kulimidwa ku Iguputo kale.
Mwina kutanthauza, “Malo Osonkhapo Moto a Paguwa Lansembe la Mulungu,” amene anali Yerusalemu.
Mawu ake enieni, “mzimu wanga.”
Palembali mawu akuti “Tofeti” agwiritsidwa ntchito mophiphiritsa monga malo oyaka moto, ndipo akuimira chiwonongeko.
“Yake” akuimira Bozira, likulu la Edomu.
Onani mawu a m’munsi pa Yes 13:21.
Kapena kuti “mkulu wa operekera chikho.”
Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”
Mbalame imeneyi ena amati “nyapwere.”
Mawu ake enieni, “choonadi.”
Umenewu ndi mtengo waukulu umene umatalika mpaka mamita 15. Umakhala ndi masamba osabiriwira kwambiri ndi nthambi zotuwa ngati phulusa.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Munthu “wosasatitsidwa” ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pa moyo wake.
Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
Ena amati “kulasa.”
Mawu ake enieni, “pabedi.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Ena amati “anthota.”
Imeneyi ndi nyama yooneka ngati hatchi.